diff --git "a/nya_mono.tsv" "b/nya_mono.tsv" new file mode 100644--- /dev/null +++ "b/nya_mono.tsv" @@ -0,0 +1,8001 @@ +input +Zipani za moyo zionekeCMD Kodi zipani zinazi zili moyo? Nthawi yofukula yakwana mzipani pamene bungwe loona mgwirizano wa zipani zosiyanasiyana la Centre for Multiparty Democracy (CMD) lalengeza zokumana ndi akuluakulu a zipani. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Bungweli laitana zipani 41 zomwe zidalembetsedwa koma zilibe aphungu mNyumba ya Malamulo. +CMD ikuchita izi kutsatira kudutsa kwa bilo yokamba za kayendetsedwe ka zipani imene mwa zina ikuti zipani zimene sizikuoneka zichotsedwe mkaundula pakatha miyezi 12. +Tenthani: Tiwaimbira Kalata yomwe CMD yatulutsa ikuti eni zipanizo atumize ku bungwelo maina a mtsogoleri wawo ndi mlembiatumizenso nambala, madera amene akukhala. +Mkulu wa bungwelo, Kizito Tenthani adati zipanizo zikatumiza maina ndi manambalawo adzawaimbira kuti akumane nawo kuti awafotokozere zomwe zili mbiloyo. +Iye adati: Ngati satiyankha mwina zisonyeza kuti kulibe munthu. Pakatha miyezi 12 ndiye kuti zisonyeza kuti chipanicho chazimirirakusonyeza kuti osindikiza zipani atha kuchifufuta. +Mwa zipani zomwe zaitanidwa ndi cha The Malawi Democratic (MDP) chomwe mwa ena amene adachiyambitsa ndi Kamlepo Kalua yemwe lero ali ku PP. +Chipani china ndi cha Malavi Peoples Party (MPP) chomwe adayambitsa ndi Uladi Mussa amene akungoyendayenda. Adali ku UDF asadasinthe golo kupita ku DPP. Madzi atachitako katondo adalumphamo kugwera mu PP, lero wasinthanso golo kubwerera ku DPP. +Titamuimbira foni ngati alembere bungweli monga iye mtsogoleri, Mussa adayankha modabwa. Malavi ndiye chiyani? adafunsa. Aaa! Nanga ine mesa ndidachokako, ndidali ku PP pano ndili ku DPP. Inuyo mungopitako mukaone atsogoleri amene apitawo osati muzindifunsa ine, adatero. +Koma Tenthani ali ndi chikhulupiriro kuti zipanizi ziwalembera. Ine ndi mkulu wa CMD, nditachoka lero sizikutanthauza kuti CMD yatha, atsogoleri otsalawo ndiwo angayankhepo ngati atafunidwa. Titsimikiza kuti mzipanizo mudatsala ena amene atilembere, adatero. +Mndandanda wa zipanizi ndi womwe udalembetsedwa mdziko muno kuti ndi zipani zokhazikika. Zina mwa zipani zoitanidwazo zidamveka pachisankho cha 1994 osamvekanso. Izi ndi monga cha Congress for the Second Republic cha Kanyama Chiume, Malawi Democratic Union cha Amunandife Mkumba, United Front for Multiparty Democracy, Malawi National Democratic Party ndi zina zotero. +Dziko lino lili ndi zipani zoposera 50. +Ulalo adali venda wa masiketi Makolo polangiza amati ukadekha, umawona maso a nkhono ndipo mwambi womwewu ansembe amati ukafuna kuvala kolona, ukuyenera kusunga khosi. +Miyambiyi siyapafupi kwa anthu ambiri kuyitsata koma umboni wake ulipo wa nkhaninkhani pakuti kwa iwo omwe adadekha nkusunga makosi, pano Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu amadziwa momwe maso a nkhono alili ndipo kolona ali mkhosi. +Edward ndi Maggie tsiku la ukwati wawo Apa pali umboni wa Edward Bannet Gangile wa kwa T/A Chiwere ku Dowa ndi Maggie Failo wa kwa T/A Malengachanzi ku Nkhotakota omwe ngakhale adakondana atangoonana koyamba, iwo adadekherana asadapalane ubwenzi. +Nthawiyo, mchaka cha 2013, Gangile adali wowerengera za chuma ku chipatala cha mishoni cha Nkhoma ndipo akuti chipatalachi chimakonda kugula katundu monga mapepala ndi zolembera kushopu ya Maggie yomwe idali ku Area 3 mumzinda wa Lilongwe. +Nthawiyo ndimayesetsa kumuthandiza mwachangu ndi mwansangala. +Timapatsana moni ndi kucheza nkhani zingapo koma ndimalephera kumuuza za kukhosi. Adandisangalatsa kwambiri ndi nsangala zomwe amandirandira nazo, adatero Gangile. +Iye adati mpata udapezeka tsiku ali mushopumo ndipo mudabwera venda ogulitsa masiketi omwe adasangalatsa Maggie ndipo mwa izi, namwaliyo adamufunsa ngati angamugulireko mkazi wake. +Ndimathokoza Mulungu kuti ndidaganiza msanga chifukwa ndidangoyankha kuti ndidzamugulira ndikadzamupeza ndipo yankholi lidamupangitsa kundifunsa mafunso ambiri pa zamoyo wanga kuphatikizapo kukayika kuti mwina ndimamunamiza, adatero Gangile. +Iye adati ichi chidali chiyambi cha awiriwa kufufuzana ndikudziwana bwinobwino mpaka adavomerezana kuti onse amadikirana kutanthauza kuti aliyense mwa iwo adadekha kapena kusunga khosi. +Iye adati awiriwa adakhala miyezi ubwenzi usadayambe kwenikweni kuchoka panthawiyo ndipo zonse zitalongosoka, adapanga chinkhoswe pa 15 April, 2015 ku Area 47 kwa azakhali a Maggie ndipo ukwati udachitikira ku Lilongwe Golf Club pa 12 July, 2015. +Chotsani chiletso chogulitsa chimanga kunjaMCCCI Bungwe loona za malonda ndi mafakitale la Malawi Confederation of Chambers of Commerce and Industry (MCCCI) lapempha boma kuti lichotse chiletso chogulitsa chimanga kunja. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Pulezidenti wa bungwelo Karl Chokotho adapereka pempholi Lachinayi potsegulira chionetsero cha malonda ku Gateway Mall mumzinda wa Lilongwe. +Iye adati chiletsochi chikupsinja kwambiri alimi angonoangono chifukwa omwe akukakamizidwa kugulitsa chimanga chawo mdziko mommuno pa mitengo yotsika poyerekeza ndi mitengo yomwe maiko ena akugulira. +Chokotho: Alimi akadapha makwacha Pa Tanzania pomwepa, chimanga chikugulidwa pamtengo okwera mwina kuposa katatu mtengo wa boma la Malawi ndiye alimi akadaloledwa kuti azigulitsa chimanga chawo mmisika ngati imeneyi, akadapha makwacha, adatero Chokotho. +Iye adati akudziwa kuti dziko la Malawi likuyenera kugula ndi kusunga chimanga kupangira zogwa chaka cha mawa zomwe sizikudziwika koma adati vuto lomwe lilipo ndi loti bungwe la Admarc lomwe limagulako bwino silikugulanso chimangachi. +Boma litakhazikitsa mitengo, alimi adali ndi chiyembekezo kuti mwina apindula pogulitsa ku Admarc koma nzosabisa kuti Admarc siyikugula chimanga moti alimi akungobwerera nacho mapeto ake mavenda akupezerapo danga, adatero Chokotho. +Nduna ya za ntchito, achinyamata, masewero ndi kuphunzitsa anthu ntchito, Francis Kasaila, yemwe adali mlendo wolemekezeka pa mwambowo, adati mpofunika kuzama ndi kukambirana bwinobwino chiletsochi chisadachotsedwe. +Ndunayo idati alimi ambiri angonoangono amadalira pologalamu ya boma ya sabuside paulimi pomwe omwe amagulitsa chimanga kunja ndi mavenda zomwe zikutanthauza kuti kuchotsa chiletsochi ndiye kuti mavenda ndiwo apindule pa sabuside ya boma. +Vuto lalikulu ndi loti omwe amagulitsa chimanga kunja ndi mavenda omwe amagula kwa alimi pamitengo yolira ndiye zikutanthauza kuti olo titachotsa chiletsochi, alimiwo sathandizika ayi agulidwabe pa mtengo olirawo ndipo mavenda ndiwo apindule, adatero Kasaila. +Osauka alibe mawu Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kwa zaka 12, ena mwa omwe akuwaganizira milandu yakupha akadali pa alimandi mndende podikira chilungamo pa milandu yoganiziridwa kuti adapha anzawo. Milanduyi, ikumatenga nthawi kuti iweruzidwe. +Izi zikusemphana ndi gawo 161 la malamulo okhudza milandu ikuluikulu lomwe limati munthu azengedwe mlandu pasanathe miyezi iwiri ndipo ngati zavutitsitsa isadutse itatu. +Komatu zodabwitsa nzoti anthu ambiri omwe akungokhala mndendewa asadaweruzidwe, alibe ndalama ndipo sangafikire owaimilira. Choncho amakhala akudikira ndondomeko ya boma pomwe anthu a ndalama zawo akapalamula, milandu yawo imayenda mwachangu chifukwa amapeza owaimira. +Mwachitsanzo, polisi ya Ntcheu chaka chathachi, idatumiza anthu 22 kundende ya Ntcheu, ndipo onsewa, palibe ngakhale mmodzi amene adakalowa bwalo la milandu. +Moyo wa kundende ndi wovuta Izi zingotanthauza kuti milanduyo yakumana ndi ya chaka chino. +Izi zikukhumudwitsa omenyera ufulu wa anthu mdziko muno. +Mkulu wa limodzi mwa mabungwewa la Centre for Human Rights Education, Advice and Assistance (Chreaa), Victor Mhango, adati ndende za dziko lino zikusungira anthu oposa 1 000 pa limandi pa milandu yoganiziridwa kupha. +Mhango adati milandu ya mtunduwu imaweruzidwa ndi bwalo lalikulu lomwe lili ndi oweruza ochepa. +Milanduyi imakhala yokwera mtengo chifukwa oweruzawa ndi omwe amayendera kuboma la opalamula mlandu. Tsopano ndi kapezedwe ka chuma, zikumavuta kuti aziyenda pafupipafupi kumakaweruza milandu ya mtunduwu, adatero Mhango. +Iye adati anthu omwe amapeza okha owaimira pa milandu sakhalitsa mndendemu chifukwa owaimirirawa amathamanga kuwapezera belo kuti zawo ziyere mwachangu. +Vuto lagona pa anthu omwe sangakwanitse kupeza owaimilira ndipo amadalira aulere ochokera nthambi ya boma ya Legal Aid. Anthuwa amaiwalika ndipo amatha zaka zambiri ali mndende, adalongosola Mhango. +Iye adati a nthambiyi alibe owaimira pa milandu ambiri zomwe zimachedwetsanso milandu. +Kuchokera chaka cha 2014 mpaka 2016 bungwe la Malawi Human Rights Commission (MHRC) lidatsogolera ntchito yothandiza kuti milandu ina iunikidwenso. Ntchitoyi yomwe inkatchedwa Kafantayeni, idathandiza kuunika milandu ya omwe adapha anzawo 154. +Malinga ndi yemwe ankatsogolera ntchitoyi Peter Chisi, milandu 161 ndi yomwe inkafunika kuunikidwa. +Iye adati ntchitoyi inkalunjika kwa okhawo omwe adapatsidwa chilango chonyongedwa atapezeka olakwa popha anzawo malamulo adziko lino asadasinthe. +Ndi ntchitoyi, anthu 131 adatuluka chifukwa adali atasewenza kale zaka zokwanira ndi chilango chomwe adapatsidwa. Ndipo tidapezanso kuti anthu atatu samayenera kumangidwa, adatero iye. +Iye adaonjezeranso kuti bungwe lake lili ndi chiganizo chopanga kafukufuku woti apeze kuti ndi anthu angati omwe akukhala mndende pokhudzana ndi milandu yopha anzawo koma asadaloweko kubwalo la milandu. +Pakufunika kuti papezeke dongosolo loti milanduyi iziyenda mwachangu chifukwa palibe chilungamo kwa olakwa ndi olakwiridwa, adatero Chisi. +Mkulu wa Legal Aid Department, Masauko Chamkakala adavomereza za mavutowa. +Anthuwa akukhalitsadi milandu yawo isadaweruzidwe. Koma kumbali yathu tikuyesetsa kuti zinthu zisinthe, adalongosola Chamkakala. +Chamkakala adati ambiri mwa anthu omwe ali pa limandi, ma failo awo akadali kupolisi. +Koma Chamkakala adati zinthu zisintha kutsogoloku chifukwa pakhala ntchito yomwe igwiridwe ndi thandizo la bungwe la European Union, yoika mafoni aulere mndende komanso polisi kuti anthu omangidwawa aziwadziwitsa okha a nthambiyi za milandu yawo. +Iye adati ntchitoyi idzayamba yoyeserera isanafalikire ndipo adatinso akupempha boma kuti awonjezere ogwira ntchito chifukwa alipo ochepa. +Mwachitsanzo, ku chigawo chonse cha mmawa kuli munthu mmodzi basi, yemwe amayendera maboma a Machinga, Zomba, Machinga ndi Balaka, adatero Chamkakala. +Pachifukwachi, Chamkakala adati bungwe lake lilowa mgwirizano ndi anthu komanso mabungwe omwe ali ndi kuthekera koimira anthu pa milandu monga sukulu ya ukachenjede ya Chancellor College ndi bungwe la Law Society mwa ena. +Iye adatinso zinthu zisintha kwambiri dziko lino likadzavomereza malamulo oti aliyense oimira anthu pa milandu azigwira ntchito yaulere kwa ma ola angapo. +Ndipo adawonjezeranso kuti afikira ku Ntcheu kuti akaone mmene zinthu ziliri chifukwa maboma ngati amenewo omwe ali kutali ndi mizinda, amaiwalika. +Mankhwala owetera nkhunda Mukadzaona khola la nkhunda, pansi pake pamakhala zibalobalo. Ena amadabwa, kodi nzachiyani? Izi akuti ndi mankhwala amene amapangitsa kuti nkhunda zisathawe. Pamene ena amati cholinga chake nchakuti nkhunda ziswane. Kodi zenizeni nziti? BOBBY KABANGO adacheza ndi mfumu Kuziona ya kwa T/A Dambe mboma la Neno yomwe ikufotokoza zambiri motere: Wawa mfumu. +Fikani ndithu. +Ndadabwa ndi zomwe zili pansi pakhola la nkhundali. Kodi nchiyani? Ndi mlerankhunda kapena kuti mankhwala oimikira nkhunda kuti ana asamafe. Amagwira ntchito zambiri pa nkhunda. +Ndi zipatso zanji? Dzina lake sindidziwa koma madera ena amangoti sopo wa mtchire chifukwa ena amachapira akasowa sopo. +Chifukwa chiyani mwamangirira zimenezi? Pali zifukwa zambiri, koma nkhani yaikulu ndikufuna kuti nkhundazi ziziswa ndipo kuti anawo asamafe. +Zichulukana bwanji oti nkhunda imaikira mazira awiri okha? Sitifuna kuti nkhunda izitenga nthawi ikhale yaikira kale ena. Inde amakhala mazira awiri omwewo koma timafuna izichita changu komanso asamafe. +Kutanthauza kuti kupanda kumanga sizingaswe? Zimaswa koma amangofa. Pamene ndamangirira zimenezi ndiye kuti sangafe ndipo azibadwa awiri awiri chifukwa choti ndamangiriranso zipatso ziwiri. +Chingachitike nchiyani mutamangirira chipatso chimodzi? Ndiye kuti atha kumabadwa mwana mmodzi. Ikaswa awiri winayo atha kufa ndipo mmodzi ndiye atsale. +Zimachitika chonchi chifukwa chiyani? Apo inenso sindidziwa koma mwina ndimo Mulungu adazipangira kuti zizitero. +Mukukhulupirira bwanji oti simukudziwa? Makolo anga akhala akugwiritsira ntchito zipatsozi pakhola la nkhunda. Ndimaona chomwe chimachitika tikati tachotsa ndiye zifukwa zokhulupirira zipatsozi zikukwanira. +Taonapo alimi ali ndi nkhunda zambiri koma sagwiritsira ntchito mankhwala, inu simukungodzinyenga apa? Nawonso ali ndi podalira, atha kukunamizani kuti sagwiritsa ntchito mankhwala pamene akudziwa pamene akudalira. Afufuzeni. +Mukachotsa chimachitika nchiyani? Kungochotsa mudabwa zikaswa ana amangofa. +Mumamangirira bwanji zipatsozi? Choyamba mukamanga khola, kayanganeni zipatsozi ndipo mumangirire. Mutha kumangirira pamene mwangomanga khola kapena nkhundazo zikangolowa kumene mkholamo. +Mumakazipeza kuti? Zimakonda kumera mumtsinje, mutasakasaka muzipeza. +Mukamangirira sichimafota? Chimafota koma musachotse chifukwa mphamvu yake imagwirabe ntchito. Ngati mwachotsa ndiye pezani zina mubwezeretsepo. +Kodi mwana atangothothola mungatani? Ndimulanga ndipo ndiyesetsa kuti tsiku lisadutse ndikayangane china. +Kodi palibe mankhwala ena? Mwina alipo koma amene makolo anga adandisiira ndi amenewa. Awa ndiye mankhwala a nkhunda amene amalera nkhunda pamudzi. +Kodi simungamangirire pakhola la nkhuku? Ayi, awa ndi nkhunda zokha basi. Mwina ena angachite koma zomwe ndikudziwa ine ndi nkhundazi basi. +Kodi khola simupasula? Zimatheka, ndipo zipatsozi timakazimangiriranso pakhola latsopanolo. +Pano muli ndi nkhunda zingati? Sizingapose 20, ndazimaliza chifukwa kanthawi kena zimaposa 50. +Kolera yaluma mano Nthenda ya kolera imene idayamba ngati njerengo mwezi wa November chaka chatha, ikukwererabe moti kuchoka Lachisanu sabata yatha chiwerengero cha anthu odwala nthendayo chidachoka pa 420 kufika pa 459 Lachiwiri. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Malinga ndi zikalata zochokera ku Unduna wa Zaumoyo, anthu 6 amwalira ndi matendawa ndipo anthu 14 akulandira thandizo mmalo apadera amene undunawo udakhazikitsa mmaboma ena. Matendawa akhudza maboma a Karonga, Kasungu, Dowa, Nkhata Bay, Lilongwe, Salima, Mulanje, Nsanje, Chikwawa, Likoma, Rumphi ndi Blantyre. +Matendawa adafala ndi msodzi wina, amene adaitenga ku Wiliro mboma la Karonga ndipo adafika nayo ku Ngala, kumene asodzi amafikira ndi kugulitsa nsomba zawo. Msodziyo adafika padokopo ali wefuwefu ndipo adachita chimbudzi mphepete mwa nyanja. +Malinga ndi Idah Msiska, yemwe ndi wapampando wa komiti ya chitukuko ya mmudzi mwa Muyereka ku Ngala, matendawa adafala kwambiri chifukwa cha kusowa zimbudzi komanso utchisi wa deralo. +Wodwala woyamba adafika pagombe nkuchita chimbudzi ndipo tizilombo tidafalikira mmadzi. Chovuta china nchoti nsomba zimaola kwambiri kumalowa ndipo zimaitana ntchentche zomwe zimafalitsa matendawa. Padakalipano tikuyendera khomo ndi khomo kuti tithane ndi matendawa ndipo amene sakutsatira malangizowa amakumalipa chindapusa, adatero Msiska. +Iye adati chodziwikiratu kuti matendawa afala chifukwa ena amachita chimbudzi mnyanja momwe enanso amatunga madzi ogwiritsa ntchito pakhomo. +Malinga ndi mmodzi mwa anthu 258 amene apezeka ndi matendawa ku Karonga, Baxter Nyondo, matendawa ndi wovuta ndipo akungoyamika Mulungu kuti akadali moyo. Iye Lachiwiri tidamupeza akulandira thandizo pachipatala chachingono cha Ngala. +Sindinkadziwa chinkandichitikira. Ndinkangothulula osalekeza. Pano bola. Ndikuyamika chifukwa achifundo adanditengera kuchipatala msanga, adatero iye. +Iyi ndi nkhani yolingana ndi yomwe adatambasula Mercy Kachepa yemwe ankadikirira mbale wake pamalo a padera a odwala kolera ku Bwaila ku Lilongwe. +Adafika kunyumba kuchoka kosewera akudandaula mmimba. Posakhalitsa adayamba kugudubuka, uku akudziyipitsira. Kupanda kuikapo mtima akadapita, adatero Kachepa. +Lolemba Nduna ya za Umoyo Atupele Muluzi idakayendera malowo komwe adatsimikiza kuti zinthu zaipa. +Nkhondo ndiye ikumenyedwa kuti vutoli lithe koma kunena zoona, matendawa atikakamira ndipo liwiro lomwe akufalira likuopsa kwambiri, adatero iye. +Muluzi adauza Nyumba ya Malamulo sabata yatha kuti katemera wa kolera yemwe boma likupereka akhoza kuthandiza kuthetsa kufala kwa matendawa ataperekedwa mmadera ambiri makamaka omwe ali pachiopsezo. +Oyanganira ntchito za umoyo mmaboma a Lilongwe ndi Karonga kumene kolera yafala kwambiri, adati sakugona tulo kaamba ka matendawa. +Woyanganira ntchito za umoyo mboma la Lilongwe, Alinafe Mbewe, adati vutoli lakula kwambiri kwa Mitengo ku Area 36 ndi Kauma komwe anthu ambiri omwe apezeka ndi matendawa amachokera. +Zinthu sizikusintha kwenikweni koma tikuyesetsabe. Kuchoka pa 28 December, 2017 kudzafika pa 23 January, 2018, anthu 35 ndiwo adapezeka ndi kolera koma kuchoka pa 24 January kudzafika pa 12 February, anthu 82 ndiwo apezeka, adatero Mbewe. +Ndipo Dr Phinias Mfune ku Karonga wati vutoli likukula chifukwa tsiku lililonse pakupezeka munthu mmodzi wotenga nthendayi. +Mphekesera zizunza anthu ku Mangochi Zina ukamva, kamba anga mwala ndithu. Anthu a mboma la Mangochi sabata yapitayi adadzuka pakati pausiku, ena mbandakucha, nkuyamba kukupa phala pokhulupirira mphekesera zoti khanda longobadwa kumene laopseza kuti yemwe sachita zimenezo awona zakuda. +Mfumu Makanjira ndi bwana mkubwa wa bomalo, Moses Mphepo, atsimikiza za nkhaniyo, koma ati sakukhulupira zoti mphepo yamkuntho yomwe yaononga nyumba, mizikiti ndi katundu mbomalo ikugwirizana ndi mphekeserazo. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Makanjira: Anthu amwa phala Mfumu Makanjira ikuti munthu wina adaitchaila lamya usiku yofotokoza kuti khanda longobadwa kumene la mdziko la Mozambique lalosera kuti mboma la Mangochi mugwa mavuto aakulu ngati anthu sakupa ndi kudya phala. +Nditatsiriza kulankhula pa lamyayo, ndinatuluka panja koma ndinadabwa kuona anthu ali pikitipikiti kukupa phala, ena akumwa. Anthu ena anafika kunyumba kwanga kukafunsa nzeru. +Tsiku lotsatira chimphepo chachikulu chidaononga nyumba, mizikiti ndi katundu wambiri moti anthu ena akuti zikugwirizana ndi mawu akhanda lija, adatero Makanjira. +Mphekeserazo zikuti khandalo, lomwe lidabadwira mdera Kumwembe mdziko la Mozambique, lidamwalira litangotsiriza kupereka uthengawo. +Mussa Malekano ndi mmodzi mwa anthu omwe adakupa ndi kumwa phalalo. Ndinalandira foni yondichenjeza kuti ndiona zakuda ndikapanda kukupa ndi kudya phala ndi banja langa lonse. +Mneneri wapolisi wa mbomalo, Rodrick Maida, adati ofesi yawo siigwiritsa ntchito zikhulupiriro pogwira ntchito, koma malamulo a dziko. +Chimphepo adati mphepo yomwe yawononga katundu ndi mizikiti mbomalo siikugwirizana ndi mphekesera za khandalo. +Ndalandira malipoti woti mphepo yaononga katundu, koma sindikukhulupirira kuti zikukhudzana ndi mphekesera za khandalo, adatero bwanamkubwalo. +Osinthasintha zipani ngosadalilikaAkadaulo Andale osinthasintha zipani ndi osadalilika, ndipo amachita izi chifukwa cha dyera, atero akadaulo ena a zandale. Koma ena mwa andalewo atsutsa izi. +Akadaulowo, Mustapha Hussein, Happy Kayuni ndi Ernest Thindwa adanena izi polankhula ndi Tamvani paderapadera potsatira mchitidwe wa andale ena wosamuka mzipani zawo ndi kulowa zina umene umachulukira makamaka nthawi ya chisankho ikayandikira. Mwachitsanzo, Lamulungu Brown Mpinganjira, Ken Lipenga ndi Henry Phoya, omwe adakhalapo nduna za boma mmaulamuliro a zipani zina mmbuyomu, adalengeza kuti alowa chipani cha DPP limodzi ndi mbusa Daniel Gunya. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mutharika (Pakati) kulandira anayiwo Lamulungu Izi zili choncho, miyezi ingapo yapitayo Sidik Mia, yemwe adakhalaponso nduna mmaboma a mmbuyomu, naye adalengeza kuti walowa MCP ndipo akufuna mpando wa wachiwiri kwa mtsogoleri wachipanicho. +Hussein adati andale osinthasintha zipani ndi wosadalirika chifukwa phindu lawo ndi losaoneka ndipo adangotsala maina okha. Iye adati anthu akudziwa kale kuti ndi wosakhazikika kotero kuwatsatira nkudzipachika wekha. +Ndimaina aphindu koma sangasinthe zinthu mchipani chifukwa cha mbiri zawo zoyendayenda. Adayamba ndale kalekale ndipo anthu amawadziwa komanso amadziwa mbiri zawo, adatero Hussein. +Polankhulapo za akuluakulu akhamukira ku DPP, Kayuni adati anayiwo akungofuna kudzawolokera pamsana pachipanicho kuti apeze mipando ya uphungu pachisankho cha chaka chamawa. +Anthuwa akuchokera mmadera momwe DPP ili ndi mphamvu ndipo akudziwa kuti kuimira chipani china pampando wa uphungu, akhoza kugwa. Iwo akungoponya khoka kozama. Komabe sitikuwadabwa chifukwa ndimo alili, watero Thindwa. +Malinga ndi Kayuni, pambali posintha zipani ngati malaya chifukwa cha dyera, vuto lina ndi la kusowa mfundo kwa zipani. Iye adati zipani za mmaiko ena zimakhala ndi mfundo zokhazikika choncho munthu amadziwiratu zomwe chipanicho chimafuna kukwaniritsa, osati kuphinduka monga zimachitira zipani za ku Malawi. +Chipani chimakhala ndi mfundo zokhazikikazimene amatsata. Koma kuno kwathu chipani chimayamba mfundo iyi, kenako nkutembenuka. Amene amatsatira mfundo imene yasiyidwa amatuluka chipanicho kukalowa china, adatero Kayuni. +Iye adati kubwera kwa alendowo kumangobweretsa chilimbikitso nthawi yochepa chifukwa ngosadalilika. Ndipo kubwera kwawo kukhonza kubweretsa nthenya mzipani akulowazo chifukwa a mkhalakale amaona ngati akufuna kulandidwa mipando. +Izi zaoneka kale kuchipani cha MCP kumene kubwera kwa Mia kwadzetsa mpungwepungwe, pomwe wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipanicho Richard Msowoya ndi akuluakulu ena adzudzula mtsogoleriyo Lazarus Chakwera pogodokera khosi kwa Mia. Asanalowe chipani cha MCP, Mia adakhalapo mzipani za UDF, DPP komanso PP. Polankhula ndi Tamvani, iye adatsutsa zoti dyera ndilo lamukokera ku MCP. +Iye adati chiyambireni ndale, sadakhaleko ndi mtima odzinthangatira yekha koma kutumikira anthu nchifukwa chake adalowa mchipani cha MCP chomwe mfundo zake nzokomera Amalawi. +Mpinganjira adali mu UDF ndipo adachoka kukayambitsa chipani cha NDA. Chipani cha PP chitalowa mboma, iye adalowera komweko koma zinthu zitavuta pachisankho cha 2014, iye adachitaya. +Iye adati mbiri yake isakhale chomuyezera pandale ndipo adati walowa DPP pofunanso kutumikira Amalawi. +Boma ili limaika mtima pamiyoyo ya anthu, nchifukwa chake ndikufuna kugwira nalo ntchito ndipo ndidzakhala nacho pamtendere ndi pamavuto pomwe, adatero Mpinganjira. +Lipenga wakhalako mmipando ya unduna kuyambira mboma la chipani cha UDF chomwe adachisiya kukalowa DPP momwenso adali nduna koma adachitsika mtsogoleri wa chipanicho Bingu wa Mutharika atangomwalira mu 2012 nkulowa PP yomwe idalowa mbwalo.Samayankha foni yake. +Phoya adayamba ndi chipani cha UDF momwe adali nduna ndipo adasintha thabwa kulowa DPP kenako adalowa MCP, kumene sadakhalitseko. Iye adafunsa kuti timutumizire mafunso, amene sanayankhe. +Milandu yachepa ku Blantyre Milandu yosiyanasiyana mu mzindawa Blantyre yatsika kuchoka pa 328 mu February chaka chatha kufika pa 204 mwezi omwewo chaka chino, atero apolisi. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Wachiwiri kwa mneneri wa polisi mu mzindawo, Dorrah Chathyoka adati iyi ndi nkhani yosangalatsa. +Kutanthauza kuti milandu yomwe anthu amapalamula yatsika ndi 37.8 pa 100 iliyonse. Iyi ndi nkhani yabwino kutsimikizira ntchito yomwe apolisi a Blantyre akugwira usiku ndi usana, adatero Chathyoka. +Iye adati polisi yawo idakhazikitsa ndondomeko zothana ndiupandu zomwe zayamba kubala zipatso. +Mwazina ndikuyendayenda komwe apolisi akuchita mmadera onse. Ena akumavala zovala za polisi ndi ena zovala zawamba kuti tithane ndi upandu, adatero iye. +Izitu zikumachitika usiku ndi usana pamene tikumayenda pa galimoto, njinga komanso ena kuyenda wapansi. Takhazikitsanso zipata mmisewu, tikumatola onse amene akuyenda nthawi yosaloledwa popanda chifukwa chenicheni, adaonjeza Chathyoka. +Iye adati zinanso zomwe achita ndikupanga ubale wabwino pakati pa apolisi ndi anthu okhala mumzinda wa Blantyre. +Tidakhazikitsa polisi yammadera, tikulankhulana bwino ndi anthu. Komanso kugawana maganizo ngati pafunika kutero. +Chathyoka adati kudzera mnjira zotere, apolisi akumanjata owaganizira kupalamula mlandu mosavuta pamene anthu akumawatsina khutu. +Anthu akupemphedwa kuti apitirize kupanga ubale wabwino ndi a polisiwa kuti nkhani yabwinoyi ichitika kwa nthawi yotalikirapo. +Cholinga ndi kupanga Blantyre wokomera aliyense, adatero. +ankawerenga nkhani pa mij Ndi mawu okha, MarcFarlane Mbewe wa Capital Radio adachiritsidwa. Awa ndi makumanidwe a mnyamatayu ndi Lisa Lamya, mtolankhani wa Yoneco FM (YFM). +Nkhaniyi idayamba mu 2014, apo nkuti Lisa akugwira ntchito ku MIJ FM. Kumeneko, namwaliyu ankawerenga nkhani. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Lero ali ndi mwana mmodzi, Evan: Macfarlen ndi Lisa Ena mwina amangomva namwaliyo akamawerenga nkhani, koma kwa MarcFarlane, zimamupatsa uthenga wina. +Mawu ake ozuna komanso Chingerezi chake chothyakuka zidanditenga mtima, adatero MarcFarlane. Ndidafunitsitsa nditapalana naye ubwenzi. Mwachangu ndidamusaka pa Facebook. Ndidamutumizira pempho kuti akhale mnzanga. +Macheza akuti adayamba. Koma mnyamatayo atapempha nambala, Lisa adamukaniza. +Ndidaponya mfundo ndipo mapeto ake adandipatsa nambalayo, adatero. +Apo zidayamba kusongola ndipo mathero ake kudali kukumana pamene mfundo zenizeni zidaumbidwa. +Lero Lisa akubwekera posankha mnyamatayu. MarcFarlane ndidamukonda chifukwa ndi ndi wanthabwala zedi koposa zonse amakonda kupemphera, idatero njoleyo. +Pamene MarcFarlane akuti: Lisa ndi mkazi wokoma mmaso komanso wakhalidwe. +Awiriwa ali ndi mwana wa miyezi isanu dzina lake Evan. Ukwati akuti apangitsa chaka chikudzachi koma chinkhoswe ndiye chidali pa 5 March 2017. +MarcFarlane, woyamba mwa ana atatu ndi wa kwa Chimaliro mboma la Thyolo. Lisa, woyamba mwa ana awiri ndi wa kwa Ben Chauya ku Ntcheu. +Zipani zisaope achinyamata Bungwe lolimbikitsa achinyamata pa ndale mu Africa la Centre for Young Leaders in Africa (CYLA), lapempha zipani zandale mdziko muno kuti zisaope kugwira ntchito ndi achinyamata. +Malingana ndi mtsogoleri wa pulogalamu yotchedwa Programme for Young Politicians in Africa (PYPA) ku bungwe la CYLA wochokera mdziko la Zambia, Anna Mate, achinyamata asakhale chiopsezo koma chitetezo pa ndale za mchipani. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mate: Achinyamata ndi ambiri Mate wati zipani zambiri zimene bungwe la CYLA lagwira nazo ntchito zimaonetsa kuti zikupereka mfundo zokhwima ndi cholinga choti achinyamata azichita mantha nkubwerera mmbuyo pa ndale. +Ife monga olimbikitsa achinyamata pa ndale tidakumana ndi akuluakulu a zipani zandale zokhazikika mdziko muno ndipo tawalimbikitsa kuti agwire limodzi ntchito ndi achinyamata pa ndale, adatero Mate. +Iye adati ali ndi chikhulupiliro kuti uthengawu wadza mnthawi yake potengera kuti nzika za dziko lino zikukonzekera kukaponya voti ya patatu chaka cha maya. +Iye adatinso zipani zomwe zatsogoza achinyamata mmaudindo zimakhala ndi mwayi waukulu wopititsa patsogolo kuchuluka kwa owatsatira potengera kuti achinyamata ndi omwe akutenga gawo lalikulu la chiwerengero cha dziko lino. +Iwo apemphanso achinyamata kuthandizana komanso kulimbikitsana pamene akufuna kutengapo gawo pa ndale. +Pakadali pano CYLA ikupitirira kufikira achinyamata ndi cholinga chowadzindikiritsa za udindo wawo pa ndale za dziko lino kuphatikizapo kuwalimbikitsa kukaponya voti pa zisankho za patatu za chaka cha mawa. +Pothirirapo ndemanga yemwe akufuna kudzaimira chipani cha Malawi Congress Party (MCP), ku Salima Gerald Phiri adati zipani zayamba kuthandiza oyimira posatengera zaka za munthu. +Atsogoleri asamangotigwiritsa ntchito achinyamata poyambitsa zipolowe basi. Nthawi yakwana yoti tigwire ntchito limodzi ndi akuluakulu popanda kuopsezedwa, adatero Phiri. +Achitira zadama mu basi Anthu ena okhala mumzinda wa Mzuzu akhala akuchitira za dama mmabasi omwe adaimikidwa kumsika wa Zigwagwa pafupifupi miyezi inayi yapitayi. +Mabasiwa, salinso mmanja mwa kampani ya Axa chifukwa banki ya FDH idawagulitsa kwa mkulu wina wa bizinesi yemwe adawaimika ku Zigwagwako poyembekezera kuwagulitsa ndi kuwaphwasula ena mwa iwo. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Imodzi mwa basi amachitiramo zadamayo Komatu anthu ena apezerapo mwayi wochitiramo za chiwerewere maka yomwe idali ndi magalasi osaonekera mkati, tintedi. +Msangulutso udatsinidwa khutu kuti izi zakhala zikuchitika madzulo komanso usiku ndipo kuti anthuwa amalipira kangachepe kuti apeze mwayi wodzithandiza mbasimo. +Komatu si anthu a zadama okhawa omwe amapumira mmabasiwo, ngakhalenso ena osowa kogona, adatenga mabasiwo ngati nyumba zogona alendo. +Pomwe Msangulutso udakazungulira pamalopo udapeza mlonda Chimwemwe Kachali yemwe adavomereza kuti wakhala akupezerera anthu akuchita chiwerewere mu imodzi mwa mabasiwo makamaka usiku. +Anthu amatengerapo mwayi chifukwa ndi yosaonekera mkati ndiye zomwe amachitazo sizimaoneka kunja. Chifukwa choti chitseko chake sichitsekeka, anthu ankangolowamo, adatero Kachali. +Iye adakanitsitsa zoti adalandirapo ndalama kuchokera kwa anthuwa. +Mwina popeza miyezi yapitayo tidalipo awiri ndi mnzanga, ndiye kuti mwina ndi yemwe amalandira ndalama; koma ine sindidalandireko kanthu chifukwa ambiri mwa anthu omwe amachitira zadama mmenemo adali anthu woti timawadziwa ndithu, adatero Kachali. +Iye adaonjezera kuti zikuoneka kuti ngakhale komwe mabasiwo adali asadagulidwe ndi bwana wake mchitidwewu umachitika chifukwa adabwera ali ndi makondomu ogwiritsidwa ntchito mwa zina. +Apa adatinso masiku ena amapezanso makondomu ogwiritsidwa kale ntchito omwe anthuwo amawataya akamaliza zadamazo. +Idafika nthawi yoti anthu amakuwa akamadutsa pano kuti mmabasimu mutuluka mwana ndipo ena amati aphwasulidwe kapena kugulitsidwa mwachangu, adalongosola Kachali. +Iye adati zitafikapo abwana ake adayesa kuitseka ndi mawaya kuti anthu asamalowe koma sizidathandize chifukwa anthuwo adadula mawayawo. +Nthawi zina ndikati ndikayendere basi pakati pausiku ndimapeza mwagona anyamata achilendo. Zikatero ndimawathamangitsa. Ambiri mwa iwo amakhala oti athamangitsidwa mnkhalango ndipo alibe kolowera, adatero Kachali. +Pocheza ndi tsamba lino, mwini ma basiwo George Biyeni adati adagula mabasi asanu omwe adali a kampani ya Axa kuchokera kubanki ya FDH ndipo adalemba alonda ake awiri oyanganira mabasiwo koma mmodzi adasiya ntchito. +Biyeni adati mphekesera yoti mmabasiwo makamaka ya tintediyo mumachitika za dama idamupeza ndipo adangoganiza zoyitseka ndi mawaya kuti anthuwo asamalowemo. +Ndimati ndikalowa mbasimo, mumaoneka kuti anthu amachitamo zawo ndithu, koma ndikafunsa sindimayankhidwa bwinobwino, adatero Biyeni. +Iye adati basi yomwe izi zimachitika kwambiriyo waiphwasula tsopano ndipo yomwe yatsala pamalopo ndi yoti omwe adawagulitsawo aikhonza kukonzekera kupita nayo ku Blantyre. +Biyeni adaonjezera kuti nzovuta anthu a zadamawa kugwiritsa ntchito basi inayo chifukwa mwini wake adaikamo anthu ake angapo omwe akugona momwemo poilondera kwinaku akuikhonza. +Ndipo polankhulapo mneneri wa polisi mchigawo cha ku mpoto Peter Kalaya adati ofesi yake sidalandirepo dandaulo pa nkhaniyi. +Tikadauzidwa tikadafufuza ndipo ochita zadamawo akadaimbidwa mlandu wa idle and disorderlykuchita zadama malo osayenera, Kalaya adatero. +Mameya afanana maloto Pamene chisankhocho cha mameya atatu a mmizinda ya dziko lino chadutsa, masomphenya a mameya onse agona polimbikitsa kuteteza malo aboma, kutolera misonkho, kulimbikitsa chilungamo pa kayendetsedwe ka ndalama komanso chitukuko. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Sabata ziwiri zapitazi, kudali zisankho za mameya pomwe makhansala a mzinda wa Mzuzu adasankha William Mkandawire wa chipani cha PP kukhala meya pomwe ku Lilongwe adasankha Desmond Bikoko wa MCP ndipo ku Blantyre adasankha Wild Ndipo wa DPP. +Ngakhale akuluakuluwa ndi osiyana zipani, Tamvani wapeza kuti pomwe amavala mwinjiro wa ufumu wa mizindayi, onse maloto awo ndi amodzi, si dale zimene zidakuta zisankhozo. +Mameya onse atatu, amene adasankhidwa patatha zaka ziwiri ndi theka kuchokera pomwe adasankhidwira mu May 2014, adati masomphenya awo ali polimbikitsa kutolera misonkho ya khonsolo, kuteteza malo a makhonsolo, kulimbikitsa kayendetsedwe kolondola Ku Lilongwe adasankha Bikoko ka chuma cha khonsolo ndi kutukula makhonsolo awo. +Mmodzimmodzi mwa iwo adaonjeza kuti iyi si nthawi yoika manja kumbuyo. +Mu teremu yoyamba, ine ndi a [meya opuma a Noel] Chalamanda tidapanga zambiri pomwe ndidali wachiwiri wawo. Pano, ngati khansala, ndipitiriza ntchito zimenezo komanso kuposerapo, adatero Ndipo. +Bikoko adati: Sindidabwere kudzasewera kapena kudzatamidwa koma kudzatumikira ndi kutukula khonsolo. Pali zambiri zomwe zikadachitika koma sizidachitike. Ntchito yanga ikhala kuchita zimenezo kuti khonsolo isinthe. +Koma Mkandawire, yemwe ndi yekhayo amene sadalandidwe mpando wa umeya adati: Ntchito ndi zomwe ndidayamba kale ndipo anthu akuzidziwa nchifukwa chake andipatsanso mwayi wina owatumikira. Ndikufuna kuwatsimikizira anthu a mkhonsolo ya Mzuzu kuti ntchito zomwe ndidayamba zipitilira, adatero Mkandawire. +Ndipo wa ku Blantyre Ndipo adangonjetsa bwana wake Chalamanda oima payekha pa chisankho chimene chidadzidzimutsa ena. Ndipo chisankho cha ku Lilongwe chidadza ndi kathumba pomwe yemwe adasankhidwa kukhala wachiwiri kwa meya, Juliana Kaduya, adazimirira ati chifukwa amaopsezedwa. +Juliana, yemwe ndi wa DPP adasinkhidwa ndi a MCP kuti ayimire pampandowo zomwe zidachititsa akuluakulu ena a DPP kuganiza kuti adali ndi kampeni kumphasa. +Akadaulo pandale ati kutayidwa kwa Chalamanda komanso kuzimirira kwa Kaduya kukusonyeza kuti ndale zidali patsogolo pa zisankhozo. +Mmodzi mwa akatswiri potanthauzira ndale, Boniface Dulani, adati zotsatira za ku Blantyre zidatengera ndale osati zintchito zamunthu. +Pakuoneka kuti anthu asankha potengera chipani osati ntchito za munthu makamaka tikatengera chitukuko chomwe Chalamanda amachita mumzindawo, adatero Dulani. +Katswiri wina, Mustafa Hussein, adadzudzula mchitidwe oopseza adindo monga momwe zidakhalira ku Lilongwe. +Adindo sangakwaniritse masomphenya awo bwinobwino ngati akugwira ntchito mwamantha. Zisankho zatha, chofunika tsopano nkuvomereza ndikuwapatsa mpata omwe adapambana kuti agwire ntchito, adatero Hussein. +Aonjezera masiku a katemera Mkulu wa oyanganira zaumoyo mu unduna wa zaumoyo Dr Charles Mwansambo wati ngakhale ntchito yopereka katemera wa chikuku wa Rubella idayenda bwino, padali mavuto ena amene adachititsa kuti aonjezera masiku opereka katemerayo. +Kuyambira pa 12 mpaka 16 June, boma lidapereka katemerayu ndipo ngakhale padali mavuto ena, ntchitoyo idayenda bwino. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ntchito iliyonse imakhala ndi zokolakola moti padali mavuto ena amene adachititsa kuti ana ena asabaidwe. Izi zidachititsa kuti tionjezere ndalama ndi nthawi ya katemerayu, adatero Mwansambo. +Iye adaonjeza kuti katemerayo ndi wofunika kwambiri. +Mkulu wa bungwe la zaumoyo la Malawi Health Equity Network (Mhen) George Jobe adati ndiwokhutira ndi momwe ntchitoyo idayendera. +Iye adati: Ntchito idayenda bwino kwambiri moti tiyamike magulu onse omwe adatengapo mbali kuti adagwira ntchito yotamandika chifukwa ameneyu ndi katemera ofunika kwambiri. +Malingana ndi mneneri wa unduna wa zaumoyo, Adrian Chikumbe, sitalaka ya aphunzitsi imene idaliko sabata yatha idapereka mpata kwa ana omwe amangokhala kuti apite kukalandira katemerayu mwaunyinji. +Zidachitika ngati kutulo. Chikonzero chathu chidali chopereka katemera kwa ana pafupifupi 8 miliyoni ndipo pofika Lachitatu sabata ya katemerayo, ana 80 pa 100 aliwonse adali atabayitsa, adatero Chikumbe. +Potengera chiwerengero chomwe adapereka Chikumbe, zikutanthauza kuti mmasiku atatu okha a katemerayu, ana 6.4 miliyoni mwa ana 8 miliyoniwo adali atalandira kale katemerayo ndipo ana 1.8 miliyoni ndiwo amayenera kulandira katemera mmasiku awiri otsalira. +Chikuku (Rubella) ndi nthenda yomwe imagwira yopumira ndipo imatulutsa zidzolo mthupi lonse ndi zizindikiro za chimfine monga kutentha thupi, kuchucha mamina ndi kutsokomola ndipo imafala popatsirana kudzera mumpweya. +Malingana ndi tsamba la zaumoyo la pa internet, chikuku (Rubella) chimayamba ndi kachilombo ka mtundu wa virus komwe nkovuta kuthana nako kwake kotero, mwana akadwala, amayenera kupatsidwa mpata wokwanira wopuma kuti asamasewere ndi anzake. +Tsambali likusonyezanso kuti ana 90 mwa 100 omwe sadalandire katemera amakhala pachiopsezo chotenga matendawa. Izi zimachititsa unduna wa zaumoyo kukhazikitsa nyengo ya katemerayu. +Tsabola ndi waphindu, wophweka kulima Ulimi wa tsabola umaoneka opanda pake komanso ogwetsa mphwayi, koma Benison Kuziona, mkulu wa Bungwe la Zikometso Innovation and Productivity Centre akuti ulimiwu ndi waphindu komanso wophweka. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kuziona adati ndi ndalama yochepa, mlimi amatulutsa ndalama zochuluka. Chaka chathachi, mbewuyi idafika pamtengo wa K3 000 pa kilogalamu ndipo alimi omwe adalima, adachita nayo mphumi kwambiri, adatero mkuluyu. +Iye adaonjezanso kuti ubwino wina wa tsabola ndi woti ukabzala chaka choyamba, chaka chachiwiri subzalanso chifukwa mvula ikangogwa mitengo ija imaphukiranso ndipo zokolola zake zimakhala zochuluka kuposa poyamba. +Tsabola ndi mbewu imene alimi ena akupindula nayo kwambiri A bungwe la Malawi Fruits mogwirizana ndi Mzuzu Agriculture Development Division (Mzadd) adachita kafukufuku wa tsabola mzaka za mmbuyomu ndipo adapeza kuti kulima tsabola ndi kophweka komanso sikulira ndalama zochuluka poyerekeza ndi mbewu zina. +Ngakhale izi zili chomwechi, president wa bungwe la Farmers Union of Malawi, Alfred Kapichira Banda, wati alimi ena atsabola mmadera ena mdziko muno amagulitsa kwa mavenda pamtengo wotsika kwambiri. Iye adati alimi ambiri sakudziwa misika yeniyeni ya tsabola kotero amangoberedwa ndi mavenda. +Tikupempha misika yovomerezeka yomwe imagula tsabolayu kuti ibwere poyera, tikufuna alimiwa azitha kugulitsa pa mitengo yabwino, adatero Kapichira Banda. +Iye adati chifukwa chakuti alimiwa akhala akugulitsa pa mitengo yotsika, ambiri akumangolima moyerekeza pomwe ena adalekeratu ulimiwu. +Bungwe la Zikometso Innovation and Productivity Centre ndi limodzi mwa mabungwe omwe amalimbikitsa za ulimi wa tsabola. Zikometso, ndi nthambi ya bungwe la National Smallholder Farmers Association of Malawi (Nasfam). +Ntchito zake ndi kugula tsabola kwa alimi, kuwagulitsa njere zabwino komanso kuwaphunzitsa momwe angalimire tsabolayu kuti azikolola ochuluka komanso wapamwamba. Bungweli lili ndi fakitale yomwe imapanga tsabola wa mmabotolo yemwe amagulitsidwa mMalawi ngakhalenso maiko akunja. +Malinga ndi Kuziona, ulimi wa tsabola umayambira ku nazale ngati momwe anthu amachitira ndi ulimi wa mbewu za masamba monga tomato. Tsabola amayenera kufesedwa kumapeto kwa mwezi wa October ndipo akuyenera kuwokeredwa pamene mvula yayamba kugwa yochuluka, adatero Kuziona. +Iye adafotokoza kuti mizere imayenera kutalikana masentimita 75 komanso pobzala, mapando amayenera kutalikirana ndi masentimita 45. +Akayamba kuphukira, amayenera kudulidwa tisonga take kuti apange nthambi zochuluka. Izi zimathandiza kuti pamtengo uliwonse mlimi adzakolole tsabola ochuluka, adatero Kuziona. +Iye adaonjezanso kuti mbewuyi imayenera kuthiridwa feteleza wa D Compound ikangobzalidwa kumene komanso CAN pakadutsa masiku 21. +Kathiridwe kake ndi kofanana ndi momwe timathirira ku chimanga. Fetelezayu amathandiza tsabola kuti akule bwino komanso abereke mochuluka, adatero mkuluyu. +Iye adaonjezanso kuti tsabolayu nthawi zina amatha kugwidwa ndi matenda komanso tizilombo. +Tizilombo tomwe timasakaza mbewuyi ndi tofanana ndi tomwe timagwira mbewu za mtundu wa masamba monga tomato ndipo mankhwala ake ndi ofanana ndi omwe amapoperedwa kumbewuzi. Mlimi akhonza kupopera mankhwala koma chachikulu ndi kubzala mbewu zabwino komanso kumapalira kuti apewe matenda ndi tizilomboti, adatero Kuziona. +Boma likonzekera Ebola Unduna wa zaumoyo wasonjola komiti yoyanganira za kapewedwe ndi kuthana ndi matenda a ebola kuti ikhale chile zitamveka kuti matendawa abuka mdziko la Democratic Republic of Congo (DRC). +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Scanning for Ebola Malingana ndi undunawu, kuyambira mwezi wa April, 2017, anthu 11 apezeka ndi matendawa mdzikolo ndipo mwa anthuwa, atatu adamwalira nawo zomwe zikupereka nkhawa kuti akhoza kusefukira mmaiko oyandikana nawo. +Dziko la DRC ndi dziko lomwe maiko osiyanasiyana kuphatikizapo Malawi amatumizako asilikali ankhondo kukathandiza kukhazikitsa bata malingana nkuti mdzikoli muli nkhondo yamgonagona. +Mkulu oyanganira ntchito zaumoyo mu unduna wa zaumoyo mdziko muno Charles Mwansambo wati komitiyi yayamba kale kugwira ntchito yake ndipo wapempha anthu kuti agwirane manja ndi komitiyi kuti matendawa asafike mdziko muno. +Komiti imeneyo yayamba kale kukumana ndi kukonza ndondomeko zoyenera. Padakalipano tayamba kale kuunika anthu olowa mdziko muno kuti ngati ali ndi matendawa abwezedwe ndipo mauthenga akumwazidwa moyenera, watero Mwansambo. +Chikalata chomwe undunawu watulutsa, chikukumbutsa anthu kuti nthendayi ndiyopatsirana ndipo imafala kudzera mu kukhudzana ndi madzi a mthupi mwa munthu amane ali ndi matendawa kapena zinyama zina zomwenso zimapezeka ndi matendawa. +Icho chati matendawa akagwira munthu, amamva zizindikiro monga kutentha thupi, kufooka, kuwawa kwa minofu, kuwawa kwa mutu ndi zilonda za pakhosi zomwe zimatsatana ndi kutsegula, kusanza, zidzolo ndi kulephera kugwira ntchito bwino kwa chiwindi ndi kapamba ndipo nthawi zina magazi amatsanyukira mkati kapena kunja kwa thupi. +Undunawu wati anthu akuyenera kusamala podwazika matenda omwe akuonetsa zizindikiro za matendawa komanso akuyenera kusamala poika maliro a munthu yemwe wamwalira ndi matenda a Ebola kuti asatengere. +Matenda a Ebola ndi amodzi mwa matenda omwe mankhwala ake sadapezeke mpaka pano ndipo unduna wa zaumoyo wati mankhwala ake aakulu nkupewa kutenga potsata malangizo a za kapewedwe. +Matendawa adabukanso mchaka cha 2014 ndipo adasautsa mmaiko ambiri ndi kupha anthu ochuluka koma chifukwa cha kugwirizana kwa maiko kudzera mu thambi ya zaumoyo ya World Health Organisation (WHO), matendawa adagonja. +Asintha mlandu wa fisi Apolisi Lachinayi adasintha mlandu wa Eric Aniva, amene adamangidwa ataulula kwa mtolankhani wa BBC kuti amagona ndi ana achichepere komanso amayi amasiye potsata miyambo ya makolo. Mneneri wapolisi mdziko lino Nicholas Gondwa adati adasintha mlanduwo kuchoka pomuganizira kugona ndi ana, kufika ku mlandu woika moyo wa wina kukhala pachiopsezo cha imfa. +Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adalamula apolisi kugwira Aniva wa zaka 40 atauza atolankhaniwo kuti adagona ndi amayi ndi ana 104 mosadziteteza potsata mwambo wa kusasafumbiumene umachitika msungwana akatha msinkhundi wa kulowakufa, umene umachitika kwa mkazi wamasiye pofuna kukhazika pansi mzimu wa mwamuna wake. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Adamangidwa: Aniva Gondwa adati akumuzenga mlandu woika miyoyo ya ena pachiswe mosemphana ndi ndime 1 komanso 2 za gawo 5 ya malamulo oti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo pantchito. Iye adati adasintha polingalira kuti ngakhale Aniva amadziwa kuti ali ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi ka HIV, iye amagonabe ndi asungwana ndi amayiwo osawauza. +Atapezeka wolakwa akhoza kulipa K1 miliyoni kapena kukakhala kundende zaka zisanu akugwira ntchito ya kalavula gaga, adatero Gondwa. +Mneneriyo adaonjeza kuti padakalipano, Aniva waulula abambo ena amene amagwira ntchito yaufisi, pomwe amalandira K3 500 mpaka K5 000 akagona ndi mayi kapena msungwana. +Aniva, yemwe adakaonekera kukhoti la Nsanje Lachinayi, akusungidwa kundende ya mbomalo pomwe apolisi akufufuzabe za nkhaniyo. +Polankhula ndi BBC, Aniva akuti adati adayamba ntchitoyi mzaka za mma 1980 ndipo wakhala akugona ndi asungwana a zaka zoyambira 12 komanso amayi amasiye. Iye adauzanso atolankhaniwo kuti amayi ndi asungwana amayamikira ntchito yake. Mkazi wake naye adati amalola amuna ake kugwira ntchitoyo chifukwa amapeza ya mchere. +Koma atafunsa ena mwa amene adagona nawo ali achichepere, adati adavulala ndipo adangolola chifukwa miyambo yawo inkaneneratu kuti ngati salola mwambowo adzadzetsa mlili mmudzimo. +Akwenya woganiziridwa kusowetsa anthu pa KCH Tsoka sasimba. Mayi wina wa ku Area 25 mumzinda wa Lilongwe adaona zakuda Lolemba lapitali atapita kuchipatala chachikulu cha Kamuzu Central (KCH) mumzindawu kukaona mwana wa mnzake woyandikana naye nyumba. +Mnzakeyu adagonekedwa mchipinda cha ana pachipatalachi. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mayiyu, yemwe apolisi sadatitchulire dzina, akuti atafika muchipindacho Lamulungu lapitali adapempherera mwana wina modabwitsa ndipo kuti pochoka, adachoka ndi mwana wodwala mmodzi pamodzi ndi womuyanganira. Awiriwo sadabwererenso mchipatalamo. +Ndipo Lolemba mayiyu atafikanso mchipindacho, anthu adamuzindikira ndipo adamukwenya kwinaku akuti ndi wa Sataniki ndipo alongosole bwino za kusowa kwa awiriwo. +Malinga ndi mneneri wa polisi ya Lilongwe, Kingsley Dandaula, anthu okwiyawo adatengera mayiyo kupolisi ya Area 33 yomwe ili pafupi ndi chipatalacho komwe mwatsoka kudalibe maofesala ndipo adaperekedwa mmanja mwa alonda apachipatalapo kuti amusunge. +Malinga ndi zithunzi zomwe taona, gulu lina la anthu lidasonkhana panja pa ofesi ya alondawo. +Dandaula adati apa mpomwe galimoto ya polisi ya Lingadzi idabwera kudzamutenga mayiyo pomuteteza ku anthu olusawo. +Koma Dandaula adatsutsa kwa mtu wa galu zoti mayiyo ngwa Sataniki. +Mayiyu ngwabwinobwino ndipo adapita kuchipatala monga zimakhalira, koma kuti adangomunamizira. Nzabodza, si Wasataniki monga anthu akunenera, adatero Dandaula. +Iye adati chifukwa cha nkhaniyi wapolisi mnzawo wa pa Area 33, adaitanidwa kukakumana ndi mmodzi mwa akuluakulu apachipatalachi Lachitatu lapitali kuti akauzidwe mvemvemve pa zomwe zidachitika patsikulo. +Polankhula ndi mkulu woyendetsa chipatalachi, Jonathan Ngoma, adati oyanganira mbali ya ana sadamuuze tsatanetsatane wa momwe nkhaniyi idayendera. +Sadandiuze momwe zidayendera patsikulo, adatero Ngoma. +Koma mmodzi mwa odikirira odwala mchipinda cha ana pachipatalachi, Jessica Phiri, yemwe mwana wake adali pabedi limodzi ndi mwana wopemphereredwayo, adati tsiku la Sabatalo, mchipindamo mudachitika zoopsa. +Phiri adati munthuyo adauza amayi onse kuti atsinzine kenako adayamba kupemphera koma pasadathe nthawi, namwino yemwe adali mchipindacho adabwera nkuuza amayiwo kuti ayangane aone zomwe amachita mayi wopempherayo. +Tidali odabwa kuona mmene amadinira pamimba pa mwanayo uku akupemphera kenako namwino uja adamuuza kuti aonetse kalata ya chilolezo chodzapempherera odwala koma adalibe ndipo adamuthamangitsa, adatero Phiri. +Iye adati posakhalitsa mayiyo adabwerera nkuyamba kukambirana ndi wodikirira mwana uja kenako adatengana ponena kuti akukadya chakudya kukhitchini, koma onse sadabwererenso. +Phiri adati mmawa mwa tsiku linzakelo mayi uja adabweranso ndipo mwamwayi adakumananso ndi namwino yemweuja koma atamufunsa za anthu omwe adatenga dzulo lake adayankha kuti sakudziwapo kanthu ndipo yankholi lidakwiyitsa anthu omwe adali mchipindamo. +Tonse tidali odabwa kuti yankho lake lidali limeneli moti anthu adayamba manongonongo kenako achitetezo adabwera nkumuuza kuti atuluke azipita koma anthu adamuthamangira akumuwowoza mpaka kumsewu, adatero mayiyo. +Namwino yemwe amanenedwayo adatsimikiza kuti iye adadabwa ndi pemphero lomwe mayiyo amachita pamwanayo nkuona adauza amayiwo kuti ayangane ndipo adati palibe wachipatala aliyense yemwe adadziwa zoti mayiyo wabwereranso atathamangitsidwa. +Tidadzadabwa kuona kuti wodwala mmodzi ndi womudikirira sakuoneka ndipo titafunsa, otsalawo adatiuza kuti munthu wopephera uja adabwerera kudzawatenga. Tidadikira koma kudali zii mpaka lero, adatero namwinoyo Lachinayi lapitali. +Iye adati pambuyo pake adangomva kuti mayi uja ali mmanja mwa apolisi a ku Area 33 ndipo pomwe amacheza ndi Msangulutso, adati sakudziwa kuti nkhaniyi yafika potani. +A Escom adziwe kuti takwiyaKapito Si zachilendonso, nyimbo yomwe aliyense akuimba ndi kuzimazima kwa magetsi. Mmalo mopereka magetsi tsiku lililonse monga anenera, ayamba kupereka mdima tsiku lonse. +Izi sizikukhumudwitsa anthu okha, nawo amabungwe akwiya nazo. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kapito: Osasekerera zimenezi Monga akunenera mkulu wa bungwe loona ufulu wa anthu ogula la Consumers Association of Malawi (Cama) John Kapito, Escom isimba tsoka posakhalitsa. +Escom imva nkhwangwa ili mmutu. Zafika pokwana ndipo tatopa ndi kulira. Uwu ndi mtopola ndipo zithera pa wina, watero Kapito. +Kapito wati vuto ndi Amalawi chifukwa safuna kugwirizana zinthu zikafika povuta monga zilili pano. +Tigwirane manja, tiyeni tionetse mkwiyo wathu ndipo awa a Escom adziwenso kuti takwiya. Si bwino kusekerera zotere, talankhula ndipo tatopa. Panopa tiyeni tichitepo kanthu, adatero Kapito. +Naye mkulu woona mabungwe a mabizinesi angonoangono lotchedwa Small and Medium Enterprises Association (SMEA), James Chiutsi, akuti chuma cha dziko lino chikutsika chifukwa makampani ambiri sakugwira ntchito. +Chiutsi wati Escom ikuyenera kupeza njira zina zothandizira anthu kusiyana nkumawanamiza nthawi zonse. +Anzathu amapanga magetsi kuchokera kudzuwa komanso kumphepo. Ife tikudalira magetsi opukusidwa ndi mphamvu ya madzi, kodi nanga madziwo akadzaphwera ndiye kuti tidzakhalanso ndi magetsi? adadabwa Chiutsi. +Panopa zinthu zaipa, makampani alowa pansi ndi pafupifupi theka. Ena atseka makampani awo chifukwa sangakwanitse kugwiritsira ntchito injini za magetsi (generator). A mabutchala nyama ikuonongeka, ometa ena asiya. Kodi dziko lingatukuke bwanji? Komanso muyembekezere kuti munthu yemweyo akuyenera kupereka ndalama ya lendi. Kodi aipeza kuti, adatero Chiutsi. +Mkuluyu ndi Kapito apempha boma kuti lichitepo kanthu pa nkhaniyi kuti Amalawi aone kusintha pa nkhani ya kuthimathima kwa magetsi. +Kalembera wa nzika wayamba Boma, kupyolera mnthambi ya National Registration Bureau (NRB), Lachitatu lidayamba gawo loyamba lolemba Amalawi kuti akhale ndi zitupa za unzika. +Gawo loyamba la kalemberayu idayamba mmaboma a Nkhotakota, Ntchisi, M chinji, Kasungu, Salima ndi Dowa. Ntchitoyi, imene ikhale mmagawo atatu, idya K36.5 biliyoni ndipo Amalawi 9 miliyoni alowa mkaundula. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ntchito ya kalemberayo ku Mchinji Lachitatu Malinga ndi mneneri wa nthambi ya boma imene ikuyendetsa ntchitoyi ya NRB Norman Fulatira, kalemberayu wayamba bwino ndipo ndiwothandiza kwambiri. +Kukhala ndi chitupa cha unzika kuthandiza mnjira zambiri. Apolisi, akaona munthu amene akumukaikira kuti ndi wakunja, azidzamufunsa kuti aonetse chitupa chake. Polembetsa anthu opindula pa ntchito za mthandizi, sabuside, nthawi ya chisankho komanso kuchipatala, Amalawi azidzangoonetsa chitupa cha unzika, adatero Fulatira. +Fulatira adatsutsa malipoti oti pali mavuto ndi malipiro a anthu omwe akugwira ntchitoyi. Iye adati boma silidalandire lipoti lina lililonse lokhudza mavuto. +Zomwe tikudziwa nzoti malipiro adachedwa masiku awiri oyambirira okha pomwe anthuwa amachita maphunziro awo chifukwa choti tidali tikuwakonzera ziphaso, adatero Fulatira. +Pamene ntchito yopereka zitupa za unzikayo yayamba, bungwe lophunzitsa anthu zosiyanasiyana la National Initiative for Civic Education (Nice) likuthana ndi mphekesera zina zimene zingafoole Amalawi kukalembetsa. +Malinga ndi mkulu wa Nice mchigawo chapakati, anthu ena akhala akufalitsa kuti kalemberayu ndi njira yothandiza kudzabera pachisankho cha 2019. +Azipembedzo ena amauzanso anthu kuti kalemberayu akusonyeza kuti dziko likutha. Ndipo ena akuti boma likungofuna kugwiritsa ntchito kalemberayu pokapemphera thandizo kumaiko a kunja. Zonsezi ndi nkhambakamwa chabe, adatero Naphiyo. +Iye adati bungwelo lifikira Amalawi ambiri pofuna kuthana ndi mphekeserazo zimene zingasokoneze ntchito ya kalemberayo. +Mkulu wa Nice Ollen Mwalubunju adati ntchito yophunzitsa anthu za kalemberayu imavuta chifukwa madera ena adali ovuta kufika. +Kudali malo ena mmaboma a Ntchisi ndi Dowa komwe sitidafikeko chifukwa nkovuta mayendedwe. Choncho tidapempha mafumu komanso aphunzitsi kuphunzitsa anthuwa za kalemberayu, adatero Mwalubunju. +Mkuluyu adatinso agwiritsa ntchito wailesi za mmadera pofalitsa uthenga. +Iye adati bungwe lake lidakumananso ndi vuto la kusowa kwa galimoto chifukwa ntchitoyi imafuna kufikira mmadera ambiri. +Kupatula apo, Mwalubunju adatinso ophunzitsa anthuwa adakumana ndi anthu a zikhulupiro zina zomwe sizilola kulembetsa. +Koma tidawalimbikitsa kuti kalemberayu ngwa aliyense ndipo kupanda kutero kukhala kusemphana ndi malamulo a dziko lino, adatero Mwalubunju. +DC wa boma la Mchinji, Rosemary Nawasha adati mbomali mudalibe mavuto ena aliwonse pokonzekera kalemberayu. +Ma Queens ndi mphatso Lolemba lapitali, mafumukazi athu, ma Queens, adali ku nyumba yachifumu ya Sanjika mumzinda wa Blantyre kumene mtsogoleri wadziko lino Peter Mutharika adawaitana ku nkhomaliro. Izi adachita pofuna kuwathokoza pantchito imene adagwira mumpikisano wadziko lonse wa Fast5. Iwo adali panambala 3. Mtsogoleri wa dziko linoyo adawapatsa asungwanawo mphatso ndi K300 000 aliyense zimene asenza pachithunzipa. +Chisankho chachibwereza chilipo pa 6 June Bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lakhazikitsa pa 6 June 2017 kuti Amalawi adzaponye voti yachibwereza kummwera cha kummawa kwa Lilongwe patangotha mwezi bwalo lamilandu la apilo litagamula kuti chisankho cha kuderali sichidayende bwino. +Chigamulochi chidaperekedwa potsatira dandaulo la yemwe ankaimira chipani cha Malawi Congress Party (MCP) Ulemu Msungama kuti chinyengo chidachitika pachisankhocho. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Voters will still use voter ID cards in 2019 Chigamulochi chitaperekedwa, zipani zandale zidapempha MEC kuti ichititse chisankho chachibwereza kuderalo msanga kuti anthu akhale ndi phungu wowaimirira ku Nyumba ya Malamulo chifukwa chigamulocho chidatanthauza kuti deralo lilibe phungu. +Pachisankho cha pa 20 May, 204, MEC idalengeza kuti Bentley Namasasu wa Democratic Progressive Party (DPP) ndiye adapambana koma Msungama adakamangala ku bwalo la mirandu za chigamulochi. +Wachiwiri kwa mlembi wa chipani cha MCP Eisenhower Mkaka, mneneri wachipani cha Peoples Party (PP) Noah Chimpeni ndi mneneri wa United Democratic Front (UDF) Ken Ndanga adati MEC isapange chidodo pa zopangitsa chisankho chachibwereza. +Mobweretsa chilimbikitso pa nkhawa ya za vuto la ndalama zopangitsira chisankhochi lomwe bungwe la MEC lidanena poyamba, bungweri lati chisankhochi chilipo pa 6 June 2017. +Potsatila chigamulo cha bwalo la mirandu la apilo, bungwe la MEC lidapangitsa msonkhano pa 4 April omwe lidafotokozera zipani ndi okhudzidwa ena kuti lipangitsa chisankho ku dera la ku mmwera cha ku mmawa kwa Lilongwe pa 6 June 2017, chidatero chikalata chomwe bungweli lidatulutsa. +Chikalatachi chidatinso pofuna kuti bungweli lisawononge ndalama zambiri, chisankhochi chichitika limodzi ndi zisankho zina monga kumpoto kwa Lilongwe Msozi, chisankho cha khansala wa kumpoto kwa Mayani ku Dedza ndi khansala wa kwa Mtsiliza ku Lilongwe. +Bungwe la MEC lati makandideti akale ndi atsopano ndi olandilidwa kupikisana nawo motsatana ndi malamulo a zisankho. +Pa zisankhozi, bungwe la MEC lati omwe adzaloledwe kuponya voti ndi okhawo omwe adalembetsa mkaundula wa 2014 ndipo sipadzakhala zosintha malo okaponyera voti. +Zipani za MCP, PP ndi UDF zati nkhaniyi ndi yabwino koma zati mpofunika kuwonetsetsa kuti pasadzachitikenso zachinyengo zomwe zingadzapangitse kuti zotsatira za chisankhochi zidzakanidweso. +Ulangizi paulimi mu 2016 Pamene tikulowa chaka chino mawa lino, ndi bwino tisanthule zina mwa nkhani zikuluzikulu komanso magawo amene tidakupatsirani mu Uchikumbe mu 2016. +Ulimi wa ziweto za mbalame Alimi ena adabwekera kuti kuweta zinziri, nkhuku za mazira komanso za Mikolongwe, nkhanga. Alimi adafotokoza momwe ziwetozi zikuwapindulira. Mwa chitsanzo, mlimi wa zinziri adati sizichedwa kukula komanso zimapirira ku matenda. Amene akuweta nkhuku za Mikolongwe adati si zibwerera pamsika komanso kuweta kwake nkosavuta. Kwa alimi a nkhanga, phindu lalikulu ndi lakuti zimaikira mazira ambiri600 pachaka, zomwe si zingatheke ndi ziweto zina za mtunduwu. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Alimi adalimbikitsidwa kupewa matope mmakola awo Malangizo paulimi Kadaulo pankhani yosunga mbewu adalangiza alimi kupewa kusunga chimanga chawo mnkhokwe za nsungwi poopetsa anankafumbwe. Iye adati chimanga chikatha, nankafumbwe amadya nsungwi ndipo mlimi akadzaika chimanga china nankafumbwe amapeza chochecheta. Alangizi enanso adatambasula za kufunika kukolola madzi pamene mvula yagwa komanso kuonetsetsa kuti akupeza mbewu ndi zina zofunikira paulimi nthawi yabwino. Adalangizanso alimi kukhala pagulu kuti asamavutike polandira ulangizi ngakhalenso kupeza misika. +Patsogolo ndi ziweto Alimi a mmadera ena mdziko muno adanenetsa kuti akusimba lokoma ndi ngombe za mkaka pamene adayamba kutsatira malangizo monga kusamalira makola, kufutsa nsipu, kubzala nsenjere, kuteteza matenda ndi zina zotero. Ndipo ena adati iwo koma akalulu amene akuthana ndi mavuto a kusintha kwa nyengo chifukwa chakudya chawo sichisowa. Kwa ena, kuweta nkhumba ndiye tsogolo labwino pomwe alangizi adanenetsa kuti kukhala ndi makola ouma, kudyetsa bwino, ndiye tsogolo lokoma la ulimiwu. Alimi ena adati koma mbuzi ndiye tsogolo labwino chifukwa sizivuta kudyetsa komanso matenda ndi ochepa. +Zipani zikufuna machawi pa chisankho Zipani zandale zati bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lichititse msanga chisankho chobwereza kudera la kummwera cha ku mmawa kwa Lilongwe kuti anthu akuderari akhale ndi phungu owayimirira ku Nyumba ya Malamulo. +Izi zikutsatira chigamulo cha bwalo lalikulu la apilo kuti chisankho cha phungu wa deralo chichitikenso litaunika dandaulo la yemwe ankayimirira chipani cha Malawi Congress Party (MCP) Ulemu Msungama kuti chisankhocho sichidayende bwino. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Sipikala wa Nyumba ya Malamulo Richard Msowoya watsimikiza kuti kutsatira chigamulochi, deralo tsopano lilibe phungu. +Bwalo lomwe lagamula ndi lalikulu mdziko muno kutanthauza kuti kulibenso komwe nkhaniyo ingalowere. Apa, zikutanthauza kuti kuderako kulibe phungu nchifukwa chake kuchitikenso chisankho, adatero Msowoya. +Pachisankho cha pa 20 May, 204, bungwe la Mec lidalengeza kuti Bentley Namasasu yemwe ankayimira chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) ndiye adapambana koma Msungama adakamangala kubwalo la milandu za chigamulochi. +Wachiwiri kwa mlembi wa chipani cha MCP Eisenhower Mkaka adati bungwe la MEC lisakoke nkhaniyo koma kuthamangitsa chisankhochi kuti anthu a mderalo akhale ndi phungu owayimilira ku Nyumba ya Malamulo. Mneneri wa chipani cha Peoples Party (PP) Noah Chimpeni adati MEC iyambirepotu kusakasaka ndalama zopangitsira chisankhochi mawu omwe adagwirizana ndi a mneneri wa chipani cha UDF Ken Ndanga. +Apa MEC iyambiretu kusakasaka ndalama zopangitsira chisankhochi munthawi yake kuti ikwaniritse ntchito yake malingana ndi malamulo, adatero Ndanga. +Chikalata chomwe MEC idatulutsa Lachitatu, chidati pali z ofunika kutsata chisankhochi chisadachitike. +Aka kakhala koyamba kuti chisankho cha mtundu uwu chichitike mumbiri ya Malawi. Motero, tikuyenera kuunika bwino chigamulochi ndi malamulo oyendetsera chisankho kuti akutinji, chidatero chikalatacho. +Mneneri wa bungwelo Sangwani Mwafulirwa adati malamulo sanena nthawi yeniyeni yofunika kutenga kuti chisankho chotere chichitike ndipo mmalo mwake akhoza kugwiritsa ntchito lamulo lomwe limati pasadathe masiku 60. +Mwafulirwa adatinso mwa zina, bungweri likufunika kuti lisake ndalama zopangitsira chisankhochi chifukwa mundondomeko ya chuma ya 2016 mpaka 2017 mulibe pologalamu yachisankhochi. +MOYO UKUTHINA Amalawi ena ati mavuto ankitsa ndipo akusowa mtengo wogwira pamene akadaulo a zachuma akuti mavutowa afikanso pena chifukwa cha njala imene ili mdziko muno. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu William Joseph wa kwa Manaseh mumzinda wa Blantyre, yemwe ndi mmodzi mwa Amalawi 62 mwa 100 alionse amene amapeza ndalama zosaposa K710 patsiku, kapena K21 000 pamwezi adati madzi afika mkhosi. +Ngakhale boma lidakhazikitsa kuti ogwira ntchito asamalandire ndalama zochepera K20 000 pamwezi, Joseph yemwe amagwira ntchito yaulonda, amalandira K15 000 pamwezi. +Bambo wa mwana mmodziyo adati: Mavuto alipo. Tikukhala nyumba ya K6 500 pamwezi, kusonyeza kuti K8 500 yotsalirayo ndiyo timagwiritsa ntchito pogula ufa wa mmawokumani, ndiwo ndi sopo. Ndiye tikumva kuti pakufunika ndalama zoposa K100 000 pamwezi kuti moyo uziyenda bwino. Ha! Malinga ndi iye, kudya ndi kawiri patsiku basi pofuna kukokera. +Umphawi wafika pena Pambali pa mkazi wake, yemwe sagwira ntchito, banja lake limasunganso mwana wina, kusonyeza kuti nyumbayo muli anthu anayi. Iye adati vuto ndi lakuti onsewo maso amakhala pa iye, kaamba koti sakwanitsa kupeza mpamba kuti mkazi wakeyo ayambe bizinesi. +Mwayi wake mwana wanga ali kusukulu ya pulaimale yomwe ndi yaulere. Khumbo langa nkuti nditapeza ndalama pafupifupi K50 000 ndipite kumudzi kukakhala apo ayi mwina ndiyambe bizinesi ngatitu ingakhale yaphindu, adatero Joseph. +Naye Bridget Yonasi, wa kwa Che Mussa mumzinda omwewu, zinthu zaima makamaka chifukwa thobwa limene amagulitsa silikuyenda malonda kaamba ka chisanu chimene chabukachi. Iye wati akuvutika kupeza chakudya, ngakhalenso kulipirira sukulu mwana wake amene ali Fomu 3 kusukulu ya sekondale ya Namiwawa. Fizi kusukuluyo ndi K5 500. +Yonasi adati ngakhale wayamba ntchito yogulitsa mgolosale komwe akulandira K10 000 pamwezi, moyo ukadali kuthina. Timagona ndi njala nthawi zambiri chifukwa chosowa ndalama zogulira chakudya. Ndimakhala nyumba ya K5 000 koma ndatulukamo chifukwa imadula ndipo ndalowa ya K3 000. Konsekotu nkuyesayesa kuti tidye komanso kupeza zofuna za anawa, adatero iye. +Nkhawazi zikudza pomwe bungwe la Centre for Social Concern (CfSC), limene mwezi ndi mwezi limatulutsa ndalama zimene zimafunika kuti munthu akhale pabwino, lati ngakhale ndalamazo zidatsikirako mwezi wa June, anthu olandira ndalama zochepa kwambiri ngati Joseph ndi Yonasi adakali pamoto. +Malingana ndi chikalata cha CfSC, ndalama zofunika pamwezi pogulira zakudya ndi zina zofunika pamoyo zidatsika kuchoka pa K166 597 mwezi wa May kufika pa K165 660 mwezi wa June. +CfSC idati nkofunika kuti boma lilimbikitse ulangizi kwa alimi kuti dziko lizikhala ndi chakudya chokwanira chifukwa njala ndi umphawi zimayendera limodzi. Bungwelo lidalimbikitsanso boma kuti lizilimbikitsa Amalawi kukhala ndi njira zopezera ndalama, mmalo mowazoloweza kuwapatsa zinthu zaulere. +Katswiri wa zachuma kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College, Ben Kaluwa adati kutsika kwa ndalama zomwe anthu angagwiritse ntchito pamwezi mwezi wa June si zodabwitsa chifukwa nthawiyi Amalawi amakhala atakolola. +Apa timayembekezera kuti ndalamayi imatsika kumene, koma taonani momwe yatsikira, palibe chiyembekezo apa kuti zinthu zikhala bwino. Ikadakhala kuti ndalamayi yacheperatu mwina tikadasangalala, koma apa yangotsika ndi ndalama yosaposa K1 000. Palibe chimwemwe, adatero Kaluwa. +Iye wati pano tili mu July kusonyeza kuti zinthu zayambanso kukwera mtengo chomwe ndi chiopsezo kwa Amalawi chifukwa zinthu zifika poliritsa miyezi ikubwerayi. +Kaluwa adati Amalawi ambiri sapeza ndalama yoposa K50 000 pamwezi ngakhale zoloserazo zikukamba ndalama yoposa K100 000. +Izi zikutanthauza kuli mavuto, ndipo tikuloweratu anthu alira koopsa chifukwa zinthu zikukwera mtengo tsiku lililonse komanso mtengo wa thumba la chimanga wakwera kwambiri, adaonjezera motero. +Mkulu wa bungwe loona za momwe chuma chikuyendera la Malawi Economic Justice Network (Mejn) Dalitso kubalasa adati mavuto onsewa akudzanso chifukwa dziko lino silikupanga katundu ochuluka. +Katundu wopangidwa mdziko amayenera kukhala ochuluka kuposa amene akumufuna kuti mtengo ukhale wabwino. Bungwe la United Nations (UN) linkawerengera kuti anthu amene amagwiritsa ntchito ndalama yosposa K710 patsiku ndiye kuti ali paumphawi ndipo onani lero ndi Amalawi angati akugwiritsa ntchito ndalama yotere? Mupeza kuti ndi ochepa, adatero Kubalasa. +Tsala bwino 2016 Pamene tikutsendera chaka cha 2016, akadaulo ena pandale ati zochitika mchakachi zikutsimikiza kuti Amalawi akuchenjera ndiye andale asamale mu 2017. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Akadanena izi kaamba ka mipungwepungwe imene idagwedeza zipani za ndale, kulephera kwa zipani zina pa zisankho zapadera zimene zidalipo komanso misamuko imene idagundika mu 2016. +Katswiri wa za ndale kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College, Boniface Dulani, adati zochitika pa dale mchakachi ndi chenjezo kwa andale kuti aunike bwino khalidwe lawo madzi asadafike mkhosi. +Masiku ano anthu adachangamuka ndipo safuna kugwiritsidwa ntchito nkutayidwa. Mikangano imene idabuka mzipani komanso zotsatira za chisankho, muona kuti ngakhale andale samayembekezera kuti zingayende choncho, adatero Dulani. +Mchakachi mudali chisankho chapadera Iye adati kale Amalawi ankatsatira ndale zofumbatitsana koma adazindikira kuti ndale zotere zimangowaphwanyira ufulu osankha atsogoleri. +Mkulu wa Malawi Electoral Support Network (Mesn) Steve Duwa adati nthawi yakwana yoti a ndale ayambe kudziyika mgulu la ena onse osati kudzipatula. +Iye adaonjeza kuti mikangano ina mzipani imayamba kaamba ka njala yofuna maudindo ndiye atsogoleri a zipani azigonjerana nkutsatira zomwe zamangidwa kumsonkhano waukulu wa zipani zawo. +Chipani cha MCP chidagwedezeka ndi mikangano mpaka akuluakulu ena adachotsedwa pomwe ena adaimikidwa. Mikanganoyo idayamba ndi apampando a makomiti a mmaboma omwe posakondwa ndi kusinthidwa kwa maudindo ena a mukomiti yaikulu, adatengera chipanichi kukhoti pofuna kukakamiza chipani kupangitsa msonkhano waukulu wosankha maudindo. +Chipanicho chidachotsa mmodzi mwa mizati yake, Felix Jumbe yemwe ndi phungu wapakati mboma la Salima pamodzi ndi akuluakulu ena monga wapampando wa mchigawo cha kummwera Chatinkha Chidzanja-Nkhoma ndi Azam Mwale. MCP idaimitsa akuluakulu Jessie Kabwira phungu wa ku Salima yemwe panthawiyo anali mneneri wachipani komanso mzati wina wa chipanicho Joseph Njobvuyalema. +Nako ku Peoples Party (PP), kudali kusamvana kwa mchipanicho kudayamba kaamba ka kubindikira kwa mtsogoleri wake Joyce Banda kumaiko akunja. +Kusowa kwa Banda kudabweretsa mikangano yolimbirana utsogoleri mchipanichi ndipo pomwe iye adasankha phungu wa kumwera kwa boma la Salima Uladi Mussa kukhala wogwirizira utsogoleri wa chipanichi, akuluakulu ena sadagwirizane nazo. +Mmodzi mwa akuluakuluwo, Christopher Mzomera Ngwira yemwe ndi woyanganira chipanichi mchigawo cha kumpoto adati njira yomwe Banda amatsata poyendetsa chipanicho idali yosokonekera ndipo iye adati kudali bwino mtsogoleriyo akadatula pansi udindo wake kuti chipanichi chione njira zina. +Akuluakulu ena a chipanicho, kuphatikizapo yemwe adaima ndi Banda pachisankho, Sosten Gwnegwe komanso Brown Mpinganjira atuluke mchipanicho. +Naye mneneri wa chipanicho Ken Msonda adatuluka PP mu September. Iye adakalowa DPP. +Anatchezera Ndimufunsirebe? Ndine mnyamata wa mu Lilongwe ndipo ndidagwa mchikondi ndi msungwana wina. Ndakhala ndikuponya mawu kwa iye koma iyeyo amayankha moti savomera kapena kundikana. Kodi ndipitirizebe kumufunsira? Ndithndizeni ndazunzika maganizo. +B, Lilongwe. +Zikomo B, Ndikuyankha molingana ndi kuti siunandiuze kuti wakhala nthawi yaitali bwanji ukuyesa mwayi wako. +Zikuoneka kuti msungwanayo sanapange chiganizo chokulola kapena kukukana. Nthawi zambiri msungwana akakhala mmalingaliro otero nchifukwa chakuti akukukayikira. Chikaikochi chikudza chifukwa pali zina zimene adamva za iwe ndiye akadali kulingalira kuti apange chisankho payekha. +Komanso iweyo mwina chidwi chako ukungoonetsa kuti ukumufuna. Tsono akalola, chotsatira chidzakhala chiyani? Mwinatu msungwanayo malingaliro ake ndi akuti akufuna kupeza mwamuna wa banja pamene iwe ukungoonetsa zizindikiro za chibwenzi basi. +Pomaliza ndiyenera kukuuza kuti ngati wayesa kumufunsira koma siukulandira yankho loyenera, bwanji osayamba wakhala mnzake nkumacheza zina ndi zina? Akuyenera kukumvetsetsa kaye kuti umaganiza chiyani, nanga umafuna chiyani asanakulole. Izo ndiye udziwe. +Mbali inayi, ungodziwanso kuti fupa lokakamoza limaswa mphika choncho ngati watha nthawi yaitali ukuyendera, ndi bwino kuyangana kwina. Nthawi siyibwerera. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Wokwatira wandipatsa mimba Zikomo Gogo, Ndinapanga chibwenzi ndi mwamuna wina amene ankaonetsa Chikondi kwambiri pa ine. +Izi zili choncho, mwamunayo sanandiuze kuti ndiwokwatuira koma nditamva kwa ena ndidamufunsa adayankha kuti akufuna kumusiya ndipo andikwatira ineyo. +Inetu ndili pasukulu ndipo zisanatheke zoti andikwatirezo, wandipatsa mimba pano akuti ndizikhala kwathu ndipo azingondithandiza. +Kodi ndipange bwanji pamenepa. +VD, Chiradzulu. +VD, Ndi ambiri asungwana ndi amayi amene ali ndi nkhani zotere. Zagwa zatha, ukuyenera kuyangana kutsogolo. +Pali zinthu ziwiri zimene ndingakulangize. Choyamba, udziwe kuti ngati wakupatsa mimba, nkhaniyi ukuyenera kuitengera kukhoti la majisitileti. Malamulo atsopano a ukwati akusonyezeratu kuti wopereka mimba nkuthawa akuyenera kubweretsedwa pamaso pa oweruza. +Kukhotiko nkomwe akatambasule kuti akuyenera kukuthandiza motani. +Chachiwiri chimene ndinganena nchakuti usataye mtima kulekeza sukulu panjira chifukwa uli ndi pathupi. Osataya pathupipo monga ena angaganizire. Ukuyenera kukabereka ndipo ukalera ndi kuyamwitsa mwana wakoyo mwakathithi, udzabwerere kusukulu. +Sukulu ndi tsogolo lako lowala ndipo udziwe kuti udzatha kuthandiza bwino mwana wakoyo moti bamboyo adzachita manyazi. Koma osaiwala kutengera nkhaniyi kukhoti. +Andipatse mimba? Agogo, Ndinali ndi chibwenzi chimene ndakhala nacho zaka 4 ndipo takhala tikugwirizana za ukwati. +Koma posakhalitsapa anangosintha nkumanena kuti akufuna andipatse mimba koma adzandikwatira zaka ziwiri zikubwerazi. Kodi pamenepo pali chikondi? Chonde ndithandizeni. +RC, Mzuzu. +RC, Apa palibepo chikondi. Akupatse mimba ya chiyani? Adzakukwatira zaka ziwiri zikatha chifukwa chiyani? Zaka 4 zonse zapitazo asanakukwatire akufuna chiyani? Udabwe nazo. Kodi anatu amayenera kukhala mphatso ya mbanja ngakhale ena angathe kukhala ndi chisankho chokhala ndi ana a mwamuna kapena mkazi amene sanakwatirane naye. +Choti udziwe, amuna ena amangofuna kukupusitsa. Uyu akhoza kukhala mmodzi mwa amuna otere. Nanga mpaka kukuuza kuti akufuna kukupatsa mimba? Nkutheka iyeyo akuuzanso akazi ena atatu chimodzimodzi. Tsono udzatani nonse mukalolera kutenga mimba kuchoka kwa iye? Khala pansi, sunthapo phanzi asakutaire nthawi. +Mmodzi adayenera kusiya ntchito Ku maintaviyu ndi komwe anthu amapezerako mwayi wa ntchito, koma kwa mtolankhani wa kanema ya Zodiak, mchigawo cha kumpoto Angela Saidi adapezerako mwayi wa banja. +Zaka 11 zadutsa tsopano kuchokera pomwe Saidi adakumana ndi mwamuna wake Isaac Banda ku maintaviyu a uofesala a kadeti ku Salima. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Isaac ndi Angela tsiku la ukwati wawo Malinga ndi Saidi, awiriwa adali asilikali ku madera osiyana ndipo amakayesa mwayi wawo wokwera pantchito, pomwe Banda adachita naye chidwi. +Apa tidayamba kucheza ngati chinzake ndithu. Padalibenso maganizo oti tsiku lina anthu nkudzavina, adatero Saidi. +Iye adati mwa awiriwo, Banda adakhonza maintaviyu ndipo adamutumiza ku Taiwan kukaphunzira za uofesala. +Saidi adati awiriwa amachezabe palamya komanso akabwera kumudzi patchuthi mpaka pomwe adamaliza maphunziro ake mchaka cha 2010. +Kwa zaka 5 tidali pa chinzake ndithu, kufikira pomwe adabwereratu ndipo ubwenzi wathu udayamba, adalongosola motero Saidi. +Iye adati apa mmodzi mwa iwo amayenera kusiya ntchito malinga ndi malamulo a asilikali oti bwana ndi juniyo sayenera kupanga chibwenzi. +Malinga ndi Saidi, iye monga juniyo, adazitaya mchaka cha 2012 atagwirako kwa zaka 10. +Phindu kawawa ndi ulimi wa tsabola Akulipirira ana awiri ku sekondale; wagula mbuzi 19 ndi nkhuku 30. Njinga, ziwiya za pakhomo komanso banja lake silikugona ndi njala. Nkhani ya Jimmy Maliwu, mlimi wa tsabola ku Mulanje ndi chitsanzo kuti ulimi wa tsabolawu ndi kawawa. BOBBY KABANGO akucheza ndi mlimiyu: Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Maliwu: Ndidagulitsa mosavuta Wawa achikumbe Wawa, imani komweko musafike pafupi, kuno ndi kwa alimi okhaokha. +Kuli chiyani mukuchita kukanizira? Tikusankha tsabola ndiye mphepo yake inuyo simungayandikire, mukuona aliyense akungoyetsemula. +Ndiye tidziwanetu Ndine mlimi wa tsabola, dzina ndine Jimmy Maliwu wa mmudzi mwa Sazola kwa Senior Chief Mabuka mboma la Mulanje. +Mudayamba liti ulimiwu? Mu 1999 ndi pamene ndidayamba kulima tsabola. +Chidachitika nchiyani kuti muyambe ulimiwu? Pa nthawiyo nkuti ndikulima chimanga komanso mbewu zina. Ndiye ndinkafuna ndichite ulimi wina womwe ndizipezerapo ndalama. Apa ndi pamene ndidasankha tsabola. +Chifukwa chiyani mudasankha ulimi wa tsabola? Ndinkafuna ulimi wa fodya, koma kuno sachita bwino. Ulimi wa tsabola ndi omwe ndidaona kuti akuphamo ndalama. +Mudayamba bwanji? Ndidalima mizere yochepa, ndimafuna kuti ndione ngati ndingathe komanso ngati msika wake uchite bwino. Zidayenda koma osati kwambiri, ndidaikamo chidwi. +Chidayenda nchiyani? Kumunda zidatheka komanso pamsika ndidagulitsa mosavutika ngakhale mtengo wake udali wolira. +Mtengo udali bwanji? Ndidagulitsa K39 pa kilogalamu pamene alimi ena amagulitsa K50. +Kuchoka 1999 kufika lero, ulimiwu ukuyenda bwanji? Mitengo ndiyo yakhala yovuta koma kumunda ndiye zonse zili bwino. Ndidaonjezera munda ndipo pano ndikulima wokula ndi mamita 35 mulitali ndi 17 mlifupi. +Munda umenewu mukukolola wochuluka bwanji? Ndikumapeza tsabola makilogalamu 150 ngati mvula yagwa bwino komanso ngati matenda sadafike. +Chaka chatha zidayenda bwanji? Nanga pamsika padali bwanji? Chaka chatha ndidakumana ndi vuto la matenda ndiye ulimi udavuta moti ndidapeza makilogalamu 45 okha chifukwa alangizi adafika mochedwa. Pamsika ndiye zidali bwino chifukwa amagula K2 500 pa kilogalamu. +Ndi matenda ati amene adavuta? Tsabola amapanga zilonda komanso mitengo imauma. Zikatere zimakhala zovuta kuti abereke bwino. Panopa matendawa tawakonzekera chifukwa tidali ndi maphunziro a momwe tingathanirane ndi matendawa. Koma vuto lomwe lidalipo kuti tikumane ndi matendawo nchifukwa cha manyowa amene tidagwiritsira ntchito. +Tsabola wakupindulirani bwanji? Muli ndalama, chaka chatha ndidapeza K112 500 kuchokera mmakilogalamu 45 amene ndidakolola. Ndagula mbuzi 19 komanso nkhuku 30. Ndili ndi ana atatu, mmodzi ali Fomu 2 wina 4 ndi wina ali ku pulaimale. Onsewa ndalama zake zikuchokera mu tsabola. Sindinagonepo ndi njala chifukwa ulimiwu umandisuntha. +Tifotokozereni za kumunda, kuli bwanji pano? Panopa tikuwokera pamene mitengo ya chaka chatha tikuthyolera kuti ipange nthambi. +Sankhani Mkandawire kulavula moto Sankhani Mkango Plus Mkandawire adachoka ku Nyasa Big Bullets chaka chino kupita ku Tanzania komwe akusewera Mbeya FC. Iye adachoka limodzi ndi Owen Chaima ndipo ulendowo udali ndi zokamba zambiri. BOBBY KABANGO adacheza naye motere: Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mkandawire: Kumalankhulidwa zambiri Tidziwe mbiri ya Sankhani Ndimachokera ku Dwangwa mboma la Nkhotakota. Ndine wachisanu mwa ana 7. Ndine wosakwatira koma posakhalitsapa mumva nthungululu. Ena amanditchula Mkango Plus, dzinali adandipatsa ndi sapota wa Bullets ati chifukwa omwetsa zigoli amavutika akakumana nane. Ndidayamba kusewera Bullets mu 2007 kuchokera ku Dwangwa United. Ndaseweranso Carara Kicks ku South Africa. +Moyo uli bwanji ku Mbeya? Zonse zili bwino, moyo ndi choncho, pena ziwawe pena kukoma koma ndili bwino. Ku Mbeya ndikusewera pafupifupi masewero alionse. +Kuchoka kwako ku Bullets padali zokamba zambiri, zidatere chifukwa chiyani? [Waseka..] Bobby aliyense amanena choncho koma pamene ndimachoka ku Bullets nkuti atagula [John] Lanjesi, [Emmanuel] Zoya komanso adali ndi [Miracle] Gabeya omwe akadagwira ntchito yanga. Kumbukiranso adali ndi George [Nyirenda]. Ndidaona kuti idali nthawi yabwino kusuntha chifukwa ndakhala ndi timuyi ilibe kanthu mpaka pamene ndimachoka itapeza ndalama. +Umawathawa anzakowa? Ayinso, koma kuona moyo wanga komanso kutimuko kumalankhulidwa zambiri zomwe zikadasokoneza tsogolo langa ndiye ndidafuna ndisunthe kuti ndikaone zina. +Tinene kuti tcheya wakale Sam Chilunga ndiye adapangitsa? [Waseka] Amene uja adali ndi masomphenya, sindingakuuzeni zambiri koma taganizani poyamba ndimalandira K33 000 ngati malipiro anga a pamwezi. Anthu amatamanda za luso langa koma kumaposedwa ndalama ndi wonenerera basi, zoona izi? Munthu uja adakweza malipiro ndiye padalakwika? Umadandaula kuti Chilunga adachotsedwa? Ndizomvetsa chisoni kumene, tinene chilungamo Chilunga adali kamuna. Adapeza ma sponsor, adakweza ndalama yolandira tikasewera gemu komanso simungamumve Chilunga akulankhula mmanyuzipepala kupempha thandizo. +Kodi ukudana ndi mtsogoleri wapanoyu Noel Lipipa? Sindikuteronso, koma Lipipa adziwe kuti akuyenera kukhala wa mphamvu chifukwa [Bullets] imakhala yosiirana. Aonetsetse kuti osewera akusangalala ndipo zikatere amupatsa zomwe akufuna, dzina lake litchulidwa paliponse chifukwa Chilunga amaganizira osewera kwambiri. +Chaponda abapondaponda Mpungwepungwe omwe udayamba nkukayikirana pa kagulidwe ka chimanga ku Zambia, wafika pamponda chimera ndi kuchotsedwa kwa George Chaponda ngati nduna ya zamalimidwe. +Mtsogoleri wadziko lino Peter Mutharika adachotsa Chaponda Lachitatu patangotha tsiku limodzi bungwe la apolisi ndi bungwe lothana ndi ziphuphu la Anti-Corruption Bureau atapeza K200 miliyoni ku nyumba ya ndunayo ku Area 10 ku Lilongwe. Ndalamazo zidali K124 miliyoni, US$57 200 (K42 miliyoni) ndi ndalama zina za ku South Africa ndi Botswana. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Adachotsedwa: Chaponda Sabata yatha, ACB idati ngakhale komiti imene Mutharika adakhazikitsa kuti ifufuze Chaponda, komanso komiti yapadera ya ku Nyumba ya Malamulo adati ACB ndi apolisi afufuze Chaponda, iwo adali atayamba kale kufufza nkhaniyo mu January. +Izi zidadza pamene komiti yapadera ya ku Nyumba ya Malamulo ndinso imene adakhazikitsa mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika zitalangiza apolisi ndi ACB kuti afufuze bwino Chaponda pakukhudzidwa kwake pa nkhani yoti boma, kupyolera mu bungwe la Admarc, litagula chimanga mwachinyengo kuchokera ku Zambia. +Chikalata chochokera kunyumba ya boma chidasonyeza kuti Mutharika adachotsa Chaponda, ndipo ntchito zake azigwira ndi Mutharika. +Pogwiritsa ntchito mphamvu zomwe malamulo amamupatsa, mtsogoleri wadziko lino Peter Mutharika wachotsa George Chaponda yemwe adali nduna ya zamalimidwe, mthirira ndi chitukuko cha madzi paudindowu, chidatero chikalatacho. +Ganizo lochotsa Chaponda labwera patapita nthawi mabungwe ndi anthu osiyanasiyana kuphatikizapo zipani zotsutsa boma zikukakamiza boma kuti lichotse mkuluyu kutamveka kuti amakhudzidwa ndi zachinyengo zomwe zikuganiziridwa kuti zidachitika pa kagulidwe kachimanga. +Poyamba, mabungwe ena adakatenga chiletso kukhothi choletsa Chaponda kupita ku ofesi kwake kapena kugwira ntchito ngati nduna, pomwe Chaponda adachotsedwa pampando wake wa mtsogoleri wa Nyumba ya Malamulo. +Zingapo zochititsa chidwi zachitika pankhaniyi, pomwe ngakhale bwalo la milandu lidalamula kuti Chaponda asagwire ntchito ngati nduna, iye adapita mdziko la Germany. Komanso, pamene kafukufuku wa makomiti awiriwo adatuluka, ofesi ya Chaponda ku Lilongwe idaotchedwa ku Lilongwe Lachitatu sabata yatha. +Popitiriza kafukufuku wake, nthambi ACB ndi apolisi adapitanso kuofesi ya Admarc ndi Transglobe. Transglobe ikukhudzidwa ndi nkhaniyo chifukwa idapatsidwa mphamvu zogula chimanga ku Zambia, zimene makomiti adadzutsa nazo nsidze kuti mwina padayenda chinyengo. +Katswiri wa zamalamulo Justine Dzonzi adauza wailesi ya Zodiak kuti malamulo a zakayendetsedwe ka ndalama mdziko muno salola munthu kusunga ndalama zakunja popanda chilolezo cha mkulu wa banki yaikulu ya Reserve Bank of Malawi. +Iye adanena izi poyankha ngati Chaponda adaswa malamulo posunga ndalama (za Malawi ndi zakunja) mnyumba mwake. +Mitsinje isefukiranso chaka chinoazanyengo Nthambi yopima zanyengo ya mdziko muno ya Department of Climate Change and Meteorological Services (DCCMS) yati chaka chino kukhala kusefukira kwa madzi, maka kuchigawo cha Kummwera. +Izi zalankhulidwa sabata yatha pamene nthambiyi idaitanitsa atolankhani kuwafotokozera momwe nyengo ya mvula iyendere chaka chino. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Nthambiyi yati pamene madera ena asowe mvula, madera okwera alandira mvula yoopsa yomwe ingachititse kuti kukhale kusefukira kwa madzi. +Zopeza za nthambiyi, zikuonetsa kuti mwayi ndi waukulu kuti madera ambiri alandira mvula yoposera mlingo wake pamene ena alandira mvula ya mlingo wake ndi ena kusoweratu mvulayi. +Nthambiyi yati pakati pa October ndi December, chigawo cha Kumpoto chili ndi mwayi waukulu wolandira mvula yabwino. Umu ndi momwenso zilili kuchigawo cha Kummwera koma mwayi wolandira mvula yambiri ndi wochuluka. +Zoloserazi zikuti miyezi ya January ndi March, zigawo ziwirizi zidzalandira mvula yambiri, zomwe zikusonyezeratu kuti kusefukira kwa madzi chaka chino ndi nkhani yosayamba. +Mneneri wa DCCMS, Ellina Kululanga, akuti nkhani ya kusefukira kwa madzi isachotsedwe chifukwa miyezi ya January ndi March ndiyo ikuopsa ndipo anthu akonzekere. +Mbali yaikulu ya dziko lino ikuonetsa kuti ilandira mvula ya mlingo wake komanso kuposera apo, adatero. +Chaka chatha mpaka kumayambiriro a chaka chino, ngakhale madera ambiri mvula sidagwe yokwanira, madzi osefulira adavuta kwina ndi kwina maka zigawo za Kumpoto (Mzuzu) komanso maboma a Chikwawa, Nsanje ndi Mulanje komwe anthu ena adataya miyoyo yawo komanso ziweto, nyumba ndi katundu zidakokoloka. +Kulandira mwana ndi nkanulo Zikhulupiriro zina ukamva, mutu wake weniweni sowe. Pali zambiri zomwe makolo amakhulupilira paumoyo wa munthu kuyambira kubadwa mpaka kumwalira. Anthu ena akuti amakhulupirira kuti mwana akabadwa, pamafunika mwambo wa nkanulo ati kusonyeza kuti mwanayo walandiridwadi pakati pa abale. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi mayi Miriam Chongwe a kwa mfumu yaikulu (T/A) Maganga mboma la Salima yemwe akufotokoza zambiri za mwambowu. +Mayi Chongwe (kumanja) kulongosola za mwambo wa nkanulo Mayi, ndati ndicheze nanu pa mwambo wa nkanulo. Mwambowu ndi wotani? Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Uwu ndi mwambo womwe umatsatidwa mwana akabadwa kusonyeza kuti abale ndi anthu pamudzipo amulandira ndipo ndi mmodzi wa iwo. Izi zimatanthauza kuti ndi mfulu kukhala ndi malo monga muja zikhalira ndi malo a banja chifukwa munthu wongobwera amavutika kupeza malo chifukwa palibe mizu yake yomwe angalondoloze. +Mwambowu umayenda bwanji? Sikuti anthu amachita kusonkhana ngati momwe miyambo ina imakhalira, ayi. Chomwe chimachitika nchakuti mwana akabadwa, chinthu choyambirira nkudziwitsa abale, makamaka amalume ake kapena azakhali, omwe amakanena kwa amfumu kenako anthu amamasuka kupita kukaona mwanayo ndi kumupititsira mphatso ngati ali nazo. +Mukati chinthu choyambirira mukutanthauzanji poti azaumoyo amati mwana akangobadwa, pompo ayamwe? Zimenezo nzoona koma apa tikukamba za mwambo. Umu ndimo makolo kalelo ankakhulupirira zinthu zisadayambe kusintha. Masiku ano miyambo yambiri ikutha pangonopangono chifukwa cha maphunziro, anthu adayamba kuzindikira kuti miyambo ina imaononga mmalo mokonza zinthu. +Tsopano mukati nkanulo timadziwa tanthauzo lokanula koma apapa pali mgwirizano wanji ndi mwambo? Eya, ndimayembekezera funso limenelo. Kumbukani kuti ndati chimakhala chinthu choyambirira mwana akangobadwa ndiye kukanulako nkutsegula mwanayo kukamwa kuti akhoza kuyamwa chifukwa walandiridwa pakati pa mudzi ndi banja lomwe wabadwiralo. +Inu mudachitapo mwambo umenewu? Mzaka za mmbuyomo nditangokwatiwa kumene koma kenako ndidazindikira kuti nkulakwa chifukwa chimakhala chilango kwa mwana. Mwachitsanzo, kumatheka kuti panthawi yomwe mwana wabadwa, palibe mayendedwe achangu malingana nkuti nthawiyo mauthenga amachita kukaperekedwa pakamwa kapena pakalata, foni kudalibe nthawi imeneyo ndiye mudikire munthu ayende kukapereka uthenga kuno mwana ali ndi njala. +Koma madotolo ndi anamwino amadziwa kuti izi zikuchitika? Sindikudziwa koma zimachitika kwambiri chifukwa chochirira kwa azamba mmidzi. Mwina ndinene kuti kukhwefula ntchito za azamba ammidzi kudathandiza nawo kuchepetsa mwambo umenewu. Sindikukhulupirira kuti dotolo kapena namwino angalekerere izi zikuchitika. +Pano zinthu zili motani? Panopa zinthu zili bwino chifukwa ndi maphunziro a zauchembere wabwino, anthu tidatsekuka mmaso. Mwina pena ndi pena zikhoza kumachitikabe poti uthenga umafika mosiyanasiyana koma nkhani yaikulu ndi yoti anthu ambiri adatsekuka mmaso chifukwa olo zokachirira kwa azamba ammidzi zidachepa. +Afufuza za mkalabongo Zambiri zakhala zikukambidwa za mkalabongo, mowa waukali umene suchedwa kutenga amene akuumwa koma tsopano, makampani 21 akufufuzidwa pamadandaulo amene Amalawi amakhala nawo. +Msabatayi, bungwe loona za chilungamo pa malonda la Competition and Fair Trade Commission (CFTC) lidatulutsa chikalata chopempha Amalawi kupereka madandaulo awo pa makampani otcheza mkalabongowo. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Akuluaku a mabungwe amene akhala akulimbana ndi mowawo, umene poyamba unkatchedwa kuti masacheti, akondwa chifukwa CFTC ikufufuza makampaniwo. CFTC idakhazikitsidwa ndi malamulo oteteza ogula mdziko lino. +Mkulu wa bungwe la Young Achievers for Development (YAD) Jefferson Milanzi adati nkhaniyi tsopano ikusongola ndipo izi zimayenera kuchitika padzana. +Dziko la Malawi ndi lalingono kwambiri choncho nzodabwitsa kuti tili ndi makampani 21 otcheza mowa umene waika miyoyo pachiswe, kusokoneza chitukuko komanso maphunziro. Iyi ndi nkhani yabwino, adatero Milanzi. +Iye adati kuchuluka kwa makampaniwo kukungosonyeza kuti amaika mtima pa ndalama zomwe amapeza, osati miyoyo ya Amalawi. +Mkulu wa bungwe lothana ndi mankhwala wozunguza ubongo la Drug Fight Malawi, Nelson Zakeyu, wati mkalabongo ndi mowa womwe umafulidwa mosatsata ndondomeko popeza ukali wake umafika 47 peresenti, omwe ndi wosavomerezeka ndi bungwe loona zaumoyo wa anthu padziko lonse la World Health Organisation (WHO). +Izi zikusemphananso ndi mfundo yachitatu ya chitukuko ya bungwe la United Nations makamaka gawo 3 ndime 3.5 yomwe imalimbikitsa umoyo wabwino pothana ndi uchidakwa, kusuta fodya ndi zina. +Akatswiri a zaumoyo a WHO omwe tikugwira nawo ntchito adatiuza kuti mowawu umaononga ubongo, mapapo, impso, komanso kulumalitsa nkhope, adatero Zakeyu. +Mkuluyu adati mkalabongo waika pachiopsezo miyoyo ya ana ndi achinyamata ambiri popeza umagulitsidwa mtengo wotsika woti aliyense atha kuufikira. +Zakeyu adati kafukufuku wa CFTC ateteza anthu ku mavuto omwe amadza akamwa mkalabongo. +Kampani zambiri zimabisa ukali weniweni wa mowawu. Zotsatira za kafukufuku wa ophunzira a msukulu zaukachenjede za ku Norway ndi Chancellor College mu 2010 adaonetsa kuti achinyamata akusokonekera chifukwa cha mkalabongo. +Malingana ndi kafukufukuyo, izi zikulimbikitsa umphawi mdziko muno chifukwa anthu omwe amamwa mowamu sakhala nzika zopanga ziganizo zothandiza potukula dziko, adatero Zakeyu. +Mchikalata chomwe CFTC yatulutsa ndipo chasayinidwa ndi mkulu wa bungweli, Wezi Malonda, chikuti CFTC yalandira madandaulo oti mowawu ulibe zizindikiro zovomerezeka ndi Malawi Bureau of Standards (MBS). +Izi zili choncho, zidakwa zina za ku Ndirande mumzinda wa Blantyre zauza Msangulutso kuti mowawu wasokoneza kwambiri miyoyo yawo. +Bright Katuli, mmodzi mwa anyamata a pamsika wa Ndirande, adati amakonda kachasu poyerekeza ndi mkalabongo. +Timamwa mkalabongo chifukwa chotsika mtengo, koma siwabwino. Mowa wina uliwonse umafuna kudyera, koma mkalabongo umachotsa chilakolako cha chakudya. Ichi nchifukwa chake ena amafa nawo. +Munthu ukamwa mkalabongo amadzuka thupi likuphwanya, komanso ali ndi ludzu lofuna kumwa wina, adatero Katuli. +Ndemwene Kazonde ndi Moses Kachisa akugwirizana ndi Katuli ndipo apempha boma kuti liletse mowawu popeza ukuononga anthu. +Sungapeze zigubu za mkalabongo pamalo omwera mowa kaamba koti umagulitsidwa mwachinyengo. Tikungomwera ugonthi, kuipa kwake tikukuona. +Mkalabongo ndi wautsiru moti panopa maso anga satha kuona bwino patali. Anzathu ena zochita nzobalalika pamene ena akulumala nkhope chifukwa cha mowawu, adateto Kachisa. +Mchikalatacho, Malonda adati: Sitikunena kuti kampani zomwe tikufufuzazi zaphwanya malamulo. Tikufuna kupeza ngati madandaulo omwe talandira ali woona, komanso ngati kampanizo zikuphwanya malamulo. Tikufuna kupeza ngati mowawu ukuonononga miyoyo ya anthu, komanso tikufuna kudziwa ngati kampanizo zikutsatira ndondomeko zonse zotetezera miyoyo ya anthu. +Kupezeka kwa chizindikiro cha MBS pamowa kumatsimikizo kuti mowawo wakwanitsa malamulo onse omwe boma lidaika pofuna kuteteza miyoyo ya anthu, yatero kalatayo. +Mafumu sanunkha kanthu pandale Kafukufuku amene achita akadaulo a zandale mdziko muno wasonyeza kuti ngakhale mafumu ena amayesetsa kusanthula momwe Amalawi akuganizira pandale, Amalawi salabadira zonena za mafumuzo. +Mmodzi mwa akatswiriwo, Happy Kayuni amene amaphunzitsa ukadaulo pandale ku Chancellor College, adati zotsatira zimene adapeza adzazikhazikitsa pa 17 March ku Sunbird Mount Soche mumzinda wa Blantyre. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mafumu sayenera kuika mlomo pankhani za ndale Izi zikudza patangotha sabata kuchokera pamene anthu ena adakuwiza Paramount Lundu pamaliro a mfumu Kabudula ku Lilongwe pomwe mwa zina adati chipani cha MCP chidalamulira dziko lino zaka 31 ndipo sichidzalamulilanso kuchokera mu 1994 pomwe chidachoka mboma. Lundu adatinso chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) ndicho chidzalamulire mu 2019. +Koma polankhula ndi Tamvani, Kayuni adati kafukufukuyo adapeza kuti mafumu amalemekezedwa ndi kukhulupiliridwa pankhani za miyambo yawo osati popanga ganizo la ndale. +Tikatulutsa zotsatirazo, anthu adzadzionera okha kuti anthu amalemekeza ndi kukhulupilira mafumu pankhani za chikhalidwe chawo koma alibe chikoka pakapangidwe ka ganizo la munthu amene asankhe pa ndale, adatero Kayuni. +Kayuni adakana kutambasula bwino kuti kafukufukuyu adamuchita nthawi yaitali bwanji, ndi anthu angati, njira yomwe adatsata pofunsa mafunso komanso mafunso amene amafunsidwa. Iye adati zonse adzazitambasula bwino akamukhazikitsa. +Iye wati chanzeru chomwe mafumu angachite nkuphathirira ku udindo wawo ndi kumalimbikira ntchito yawo mmalo motaya nthawi ndi zandale powopa kutsukuluza ulemu omwe ali nawo. +Pa zomwe mafumu ena akhala akunena kuti amayenera kukhala mbali yaboma, Kayuni wati ichi nchilungamo chokhachokha koma waunikira kuti mpofunika kutanthauzira bomalo molondola. +Mpofunika kutanthauzira bwinobwino liwu lakuti boma chifukwa mwina mafumu oterowo amaona ngati boma nchipani cholamula pomwe si choncho. Boma limagawidwa patatu: Mtsogoleri ndi nduna zake, aphungu a Nyumba ya Malamulo komanso mabwalo oyendetsa. +Akamati amakhala mbali ya boma, sakulakwa koma aziganizira tanthauzoli kuti iwo ngopanda mbali ndipo ntchito yawo nkutsogolera anthu awo pankhani zamakhalidwe ndi chitukuko. Ndale nza anthu ena, adatero Kayuni. +Polankhula ku maliro a T/A Kabudula, Senior Chief Lundu adaweruziratu kuti chipani cha DPP ndicho chidzapambane pachisankho cha 2019 ndipo kuti kaya wina afune kaya asafune, mafumu ena mdziko muno sadzaleka kusapota mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika ndi chipani cha DPP. +Ngati tili pansi pa ulamuliro wa Mutharika ndi chipani cha DPP, chotiletsa kumusapota nchiyani? Choti mudziwe nchakuti chipani cha DPP chikuyenera kulamula mpaka 2019 ndipo chidzapitiliza kuchoka apo, adatero Lundu kumaliroko. +Iye adapitiriza kunena kuti chipani cha Malawi Congress Party (MCP) chomwe mtsogoleri wake Lazarus Chakwera adali pa maliro pomwepo chisamalote zodzalamuliranso ndipo kuti kwake kudatha momwe chidatuluka mboma ngati chipani cholamula. +Chakwera atafunsidwa ndemanga yake ndi Tamvani pa nkhaniyi adati alibe mau aliwonse kenako nkuseka. +Oyendetsa nkhani za mafumu ku unduna wa Maboma angonoangono Lawrence Makonokaya adati timutumizire mafunso omwe tikuyembekezera mayankho ake. +Zotsalira Tikuchezanso ndi kadaulo wina amene adacchita nawonso kafukufukuyo. +Amabungwe akukonzanso zogwirira ntchito limodzi Pozindikira kuti mutu umodzi susenza denga, mabungwe omwe si aboma omwe akugwira ntchito zosiyanasiyana mdziko muno, kuphatikizapo za maufulu a anthu komanso kayendetsedwe ka boma, ati ali ndi cholinga chokhazikitsa ndi kulimbikitsa mgwirizano pakati pawo kuti azitha kugwira ntchito limodzi pofuna kutumikira mtundu wa Amalawi pa zofuna zawo. +Mmodzi mwa akuluakulu a mabungwe omenyera ufulu wa anthu ndi kudzudzula zolakwika pakayendetsedwe ka zinthu, McDonald Sembereka, adatsimikizira Tamvani kuti mabungwe angapo avomera kale kulowa nawo mumgwirizanowu ndipo posachedwapa uyamba kugwira ntchito yake. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Cholinga chathu nchimodzi basi monga oyimirira Amalawi kuonetsetsa kuti zinthu zikuyenda bwino ndipo Amalawi sakuvutika kapena kuphwanyiridwa maufulu awo osiyanasiyana. Taganiza izi poona momwe zinthu zayamba kuyendera mdziko muno, adatero Sembereka. +Koma katswiri wa zamalamulo ndi ndale Blessings Chinsinga wati zomwe akulingalira mabungwewa zingatheke pokhapo atasintha khalidwe ndi magwiridwe a ntchito zawo kuti athe kuongolera ndi kudzudzula kayendetsedwe ka zinthu mdziko muno. +Tamvani itamufunsa maganizo ake pa lingaliro la mabungwewa, Chinsinga adati ngakhale ganizoli ndi labwino pachitukuko ndi tsogolo la dziko lino, mabungwewa ali ndi ntchito yaikulu yomema Amalawi kuti awakhulupirirenso potengera momwe zinthu zakhala zikuyendera mmbuyomu. +Ndi ganizo labwino koma lovuta kukwaniritsa chifukwa kuyamba nkuyamba, pali kusagwirizana pakati pa mabungwe eni ake. Izi mukhoza kutsimikiza potengera momwe ntchito za mabungwewa zakhala zikuyendera, makamaka pokonza zionetsero, adatero Chinsinga. +Iye adati Amalawi ambiri adataya chikhulupiriro kuchokera mchaka cha 2011 pomwe atsogoleri a mabungwe adamema zionetsero za dziko lonse koma mapeto ake anthu ena adaphedwapo ndipo patangopita nthawi pangono mabungwewa adakhala chete. +Zionetsero za 2011 ndizo zidali nsanamira yaikulu ya mabungwe yosonyeza mphamvu, kugwirizana ndi mtima wofunadi kuthandiza, koma zomwe zidachitika zija zidagwetsa anthu ulesi waukulu moti pano ambiri alibenso nazo chidwi [zochita za amabungwewa], adatero Chinsinga. +Iye adati chofunika apa nkuyamba apanga mfundo imodzi yomwe ingaonetse kuti cholinga chawodi nchimodzi, apo ayi, palibe chomwe angapindulepo. +Koma Sembereka wanenetsa kuti mgwirizano wa ulendo uno ukhala wosiyana ndi migwirizano ina yonse mmbuyomu kaamba koti mfundo zake zikhala zakupsa ndi zomanga komanso zotengera maganizo a anthu ndi kudalira zokambirana mmalo mongolozana zala. +Amalawi ena omwe alankhula ndi Tamvani ati chimawagwetsa ulesi kwambiri nchakuti atsogoleri a mabungwewa sachedwa kutembenuka akalonjezedwa kapena kupatsidwa maudindo mboma lolamula. +Lameck Silungwe wa ku Chitipa adati nzokhumudwitsa kuti amabungwe amakokomeza kuti iwo ndi omenyera ufulu anthu ndi kudzudzula pomwe boma likulakwitsa koma mapeto ake amaoneka ngati iyi ndi njira yopemphera maudindo mboma. +Ndi atsogoleri angati a mabungwe omwe adapereka chiyembekezo mwa Amalawi kenako nkutseka pakamwa Amalawiwo akuwafuna kwambiri? Ndi ochuluka oti mwina enafe sitingathe kuwalakatula onse. Zimenezi ndizo zimagwetsa ulesi, adatero Silungwe. +Masozi Banda wa mboma la Nkhata Bay naye adati adali ndi chiyembekezo chachikulu kuchokera kwa amabungwe pa zomwe adachita mchaka cha 2011, koma kenako adaona ngati wagwiritsidwa ntchito nkutayidwa ngati wopanda phindu. +Anthu ambiri tidalolera kupita kukapanga zionetsero mmizinda chifukwa cha chikhulupiriro koma patangotha miyezi yochepa chabe, atsogoleri ambiri adayamba kulowera kosiyanasiyana kutisiya manja ali mkhosi, adatero Banda. +Naye Manuel Sajiwa wa mboma la Lilongwe adati akhoza kutsatira mabungwewa pokhapokha ataonadi kuti pali cholinga chenicheni osati kufuna kupanga phokoso longolambulirapo njira yopezera maudindo. +Zimayamba chonchi, amabwera pangonopangono nkumatitsimikizira kuti akudzatitsogolera kuti timenye nkhondo ya ufulu wathu koma posakhalitsa umangomva kuti anthu ochepa, makamaka iwowo, ali mmaudindo kenako zii, adatero Sajiwa. +Zitachitika zionetsero za 2011 zomwe adatsogolera akuluakulu a mabungwe oima paokhawa, anthu ambiri adaphedwa pazipolowe zomwe zidabuka pakati pa apolisi ndi anthu pomwe apolisi adaletsa anthu kuononga katundu wa eni. +Patangotha miyezi yochepa chichitikireni izi, atsogoleri ena a mabungwe adapatsidwa maudindo mboma latsopano la PP ndipo izi zidakhalangati zasokoneza mgwirizano wa mabungwewa omwe adayamba kugwira ntchito paokhapaokha. +Ena mwa akuluakulu a mabungwe omwe adalandira maudindo kuchoka mchaka cha 2011 ndi Sembereka, yemwe adapatsidwa udindo wa mlangizi wa pulezidenti pankhani za mabungwe mboma la Joyce Banda wa chipani PP; Dorothy Ngoma, womenyera ufulu yemwe adapatsidwa udindo woyanganira za uchembere wabwino mboma lomwelo la PP; ndipo mboma latsopano la DPP, mmodzi mwa amabungwe omwe adakhala chete atapatsidwa udindo ndi Mabvuto Bamusi, yemwe ndi mlangizi wa Pulezidenti pa zamabungwe omwe si aboma. +Malingaliro a Khirisimasi Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Khirisimasi ndi Januwale Zalowa mmanyumba (adalakwitsa ndi oimbayo osati in Tadeyo) Zaseseratu! Kwa amene adaliko nthawi imene Kennedy Ndoya, ankatchuka kuti Madolo akhoza kuyikira umboni kuti ikafika nyengo ya Khirisimasi ngati ino, nyimboyi siyimasowa pawailesi. +Abale anzanga, inde, iyitu ndi nthawi yachimwemwe, chisangalalo. +Ndimakumbuka nthawi imeneyo ndikadali kwathu kwa Kanduku nthawi ino ndiye kunkakhala kulima maganyu osati masewera kuti tipeze ndalama zosangalalira. Ndani safuna kudzipepesa. +Ife ndiye tatsekera kale kuntchito. Tikayambanso ntchito chaka cha mawa, adatero mkulu amene adali ndi Abiti Patuma. +Koma phwando la kuntchito kwanu lija ndiye ndewu zinaliko. Majuniyo kuswana ndi mabwana. Chikondi nacho chinali kuonetsedwa pakati pa majuniyo ndi mabwana awo pamdima komanso mgalimoto, adatero Abiti Patuma. +Pajatu Abiti Patuma samayimva nkhani ya maphwandoyi. Ndithu pakadalipano sindikudziwa kuti chaka chino walowa mmaphwando a makampani angati! Iwe phwando la kuntchito, ngati sunafike pomenyana ndi abwana wako ndiye kuti phwandolo silinathe, adatero mkulu uja. +Koma kunavuta zedi. Abwana kuvina ndi sekilitale, mkazi wabwana zibakera mwa sekilitale! Ngodya zomanga phwando la kuntchito, adatero Abiti Patuma. +Ukudziwa kale. Kumwa zimene sunamwepo. Kusakaniza zakumwa. Ngati sudzimbidwa ndi nyama yootcha ndiye kuti kuphwandoko sunapiteko, adabwekera Gervazzio. +Nkhani zili mkamwa, adatulukira mnyamata atavala malaya a blue, ojambulapo zitsononkho zinayi. Iye adali ndi chimwemwe kutsaya. +Dizilo Petulo Palibe ndiye mafumu! Lamulo lolola Paparazzi ndi anzake kupeza mauthenga mosavuta yadutsa mu ulamuliro wa Moya Pete, adadi, adatero mkulu uja. +Abiti Patuma adangoti kukamwa yasaaa! Ndipo Male Chauvinist Pigs isachite matama ngati idakambapo kanthu zopatsa ufulu Paparazzi ndi anzake, adapitiriza. +Kodi mkulu, si Dizilo Petulo Palibe yomweyo imene idasintha zina ndi zina lamulolo lisanalowe mkanyumba komata? Si inu nomwe mudasintha lamulolo kuti zinthu zizikukomeranibe pomwe mukulamula, mwaiwala kuti zidzakugwirani pakhosi mukadzasiya kulamula pano pa Wenela? adafunsa Abiti Patuma. +Koma zonse zili apo, kudutsa kwa lamulolo kapena ayi, kwa ine palibe kusintha. Lamulo si lamulo basi? Lamuloli lidzachititsa kuti kukhazikitsidwe Public Information Commission yoti izidzathandizira kukwaniritsa lamuloli. +Kunjakutu kuli Human Rights Commission, koma ufulu wa anthu siukuphwnyidwa? adfunsa mkulu adali ndi Abiti Patuma uja. +Fodya wakunja wayamba kulowa Pomwe dziko la Malawi lalima fodya wochepa ndi makilogalamu 27 miliyoni pamlingo omwe ogula fodyayu adaitanitsa, mavenda ena amachawi ayamba kulowetsa fodya kuchoka mmaiko oyandikana ndi dziko lino. +Fodyayu akumalowetsedwa pogwiritsa ntchito njira zozemba chifukwa mchitidwewu ngosemphana ndi malamulo a dziko lino. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Wogwirizira udindo wa mkulu wa bungwe loyendetsa ulimi wa fodya mdziko muno la Tobacco Control Commission (TCC) David Luka adati bungwe lake likudziwa za mchitidwewu ndipo lidatumiza maofesala ake kumalo onse omwe izi zikuchitika. +Maofesala athu ali ku Nkhamenya, mboma la Kasungu komwe kumalowera fodya kuchokera mdziko la Zambia ndipo ena ali ku Mchinji komanso ku Namwera mboma la Mangochi komwe fodya wake amakhala ochokera ku Mozambique, adatero Luka. +Iye adati bungwe lake ndi lokhumudwa ndi mchitidwewu omwe uli vuto lalikulu pa ulimi wa fodya mdziko muno. +Ntchito yoyesetsa kuti fodya asalowe kapena kutuluka mdziko muno siyapafupi, ndipo sikwapafupi kuchitapo kanthu adatero Luka. +Iye adaonjezeranso kuti nkhanizi kwambiri ndi zokhudza dziko ndi dziko linzake. +Alimi a fodya ena mboma la Mchinji adatsimikiza za kulowa kwa Fodya mdziko muno. +Mmodzi mwa alimiwa, Lazarus Chitedze, yemwe wakhala akulima fodya kwa zaka pafupifupi 20 adati fodyayu akulowa pangono chabe kuchokera mdziko la Zambia kusiyana ndi momwe zimakhalira zaka zonse. +Akulowetsa fodya ndi mavenda angonoangono omwe amagwiritsa ntchito njinga, mwina chifukwa chakuti mmaliremu muli asilikali omwe akulondera chimanga kuti chisatuluke, adatero Chitedze. +Iye adati chaka ndi chaka fodya amalowa kuchokera ku Zambiako kapena kutuluka kuchoka mdziko muno. +Zimatengera komwe msika uli bwino chaka chimenecho.Ngati ku Zambia zili bwino, mavenda amazembetsa fodya kupita naye komweko, adatero Chitedze. +Iye adati zikatere zimawakomera alimiwa chifukwa mavendawa amawagula mokwera mtengo kusiyana ndi ku msika wa fodya. +Malinga ndi Chitedze, chiopsezo chimakhalapo fodya akamalowa kuchokera mdzikolo chifukwa zikhonza kuchulutsa fodya pamsika kuposera mlingo omwe ogula akufuna. +Polankhulapo mlimi wina yemwe sadafune kutchulidwa dzina lake adati fodyayu akulowa pangono chifukwa ku Zambiako ayamba kumene kusankha fodya. +Akangoti wafika pachimake kumeneko, timuona akulowa wochuluka zedi, adatero mlimiyo. +Mwezi wathawu, woyanganira dera la kummawa mboma la Zambia Chanda Kasolo adauza ena mwa atolankhani a dzikolo kuti asilikali omwe ali mmalire a dziko lino ndi dzikolo akutetezanso kuzembetsa fodya. +Dziko la Zambia lidalengeza chaka chathachi kuti likweza mlingo wa fodya yemwe amalima kuchoka pa ma kilogalamu 23 miliyoni kufika pa 30 miliyoni chaka chino. +Ndipo chaka chathachi mtsogoleri wa bungwe la alimi la Eastern Fodya Association of Zambia (Efaz) Franklyn Mwale adadandaulira bungwe loyendetsa ulimi wa fodya mdzikolo kuti msika wawo amautsekula mochedwa poyerekeza ndi wa dziko lino. +Koma limodzi mwa mabungwe a alimi la Tobacco Association of Malawi (Tama) lidati silidalandire lipoti lililonse lokhudza kulowa kwa fodya kuchokera mdziko la Zambia. +Apha mkazi ndi apongozi kaamba kothetsa banja Mnyamata wina wa ku Mangochi wagwa mmanja mwa apolisi atapha mkazi ndi apongozi ake kaamba kothetsa banja. +Stephen Sani wa zaka 25 adavomera mlandu wopha mkazi wake Annie Smoke ndi apongozi ake, Enifa Smoke, ndipo pomwe timasindikiza nkhaniyi nkuti iye akuyembekezera kukaonekera ku khoti. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Sani adati adachita zaupanduzo kaamba koti makolo a mtsikanayo adathetsa banja lake ndi cholinga choti akapitirize maphunziro. +Mayi ndi gogo wa ophendwawo, Alida Moyenda, adati awiriwo adalowa mbanja atachimwitsana. Panthawiyo nkuti Annie ali ndi zaka 16, komanso ali folomu 1. +Gogo Moyenda adati poona kuti mtsikanayo adali wamngono, komanso wanzeru kwambiri pamaphunziro adaganiza zomubwezera kusukulu, koma mwamunayo adakana. +Timafuna Annie apitirize maphunziro, koma popeza mwamunayo amakana tidangoganiza zothetsa banja kuti pasakhale kupingana kulikonse, adatero gogoyu. +Iye adati banja la awiriwo lidatha pa August 5 2017 ndipo mtsikanayo adakayambiranso sukulu. Gogoyu adati banja la Sani ndi Annie mudalibe mavuto ena aliwonse, koma chomwe makolowo amafuna ndi choti mkaziyo aphunzire. +Padalibe mavuto ena aliwonse, koma chomwe chimatikhudza nchoti mtsikanayo adali wangono woyenera kukhala pasukulu osati pabanja, adatero Moyenda. +Mneneri wa polisi wa mboma la Mangochi, Amina Tepani Daudi, adati pa August 13 2017 Annie ndi amayi ake adatengana ulendo wokaona mbale wawo wina mmudzi mwa Mbapi mboma lomwelo. +Popeza mwamunayo amakhala moyandikana ndi makolo amtsikanayo, adadziwa za ulendowo ndipo adawatsatira mpaka pa famu ya Funwe pomwe adawaimitsa ndi kuwachita chiwembu. +Titalandira uthenga woti mu famu ya Funwe mwapezeka mitembo iwiri, tidaitengera ku chipatala chachingono cha Monkey Bay komwe adatiuza kuti anthuwo adamwalira kaamba ka kutaya magazi kwambiri atabaidwa ndi mipeni pakhosi, adatero Daudi. +Iye adati apolisi adagwira Sani pomuganizira kuti ndiye adachita zaupanduzo. Atamufunsa, adavomera mlanduwo moti akuyembekezera kuyankha mlandu wakupha womwe ukutsutsana ndi ndime 209 ya malamulo a dziko lino. +Akapezeka wolakwa, Sani akagwira ndende moyo wake wonse. +Mkazi wa mtsogoleri wa dziko lino, Gertrude Mutharika, wakhala akulimbikitsa atsikana omwe adalowa mbanja akadali a angono kuti abwerere kusukulu. +Malingana ndi kafukufuku wa mabungwe osiyanasiyana kuphatikizirapo la UNDP, atsikana ambiri mdziko muno amalowa mbanja asadafike zaka 18. +Mkulu wa bungwelo, Dan Odallo, adati vutoli ndi lomwe likuchititsa kuti atsikana ambiri azisiira panjira sukulu. +Pafupifupi theka la atsikana a mdziko muna amalowa mbanja asadafike zaka 18, adatero Odallo. +Pofuna kuthana ndi vutoli, Nyumba ya Malamulo idakhazikitsa malamulo woti atsikana azilowa mbanja akakwana zaka 18 kapena kupotsera apo. +Mafumu asalidwa pogawa chimanga Ntchito yogawa chakudya kwa anthu osoweratu pogwira ili mkati koma kafukufuku wathu wasonyeza kuti mafumu sakukhutira ndi momwe ntchitoyi ikuyendera makamaka pa kasankhidwe ka anthu olandira chakudyachi. +Kafukufukuyu wapeza kuti mabungwe ambiri omwe akuthandizana ndi boma pa ntchitoyi akusankha okha anthu oti alandire chakudya ndipo nthambi yolimbana ndi mavuto ogwa mwadzidzidzi ya Department of Disaster Management Affairs (DoDMA) yati njirayi ichepetsa katangale. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Akuti midzi yambiri yasiyidwa: Lukwa Mmbuyomu, mbiri ya ntchito yogawa chakudya kapena zipangizo zina mmidzi pogwiritsa ntchito mafumu ndi makomiti a mmidzi idada ndi nkhani ya katangale pa kasankhidwe ka anthu olandira. +Koma mafumu auza Tamvani kuti njira yomwe ikutsatidwa tsopanoyi ndiyo ingapititse patsogolo katangale chifukwa anthu osayenera kulandira akhoza kupeza danga kaamba koti olembawo sakudziwa za mmadera. +Tikungomva kuti anthu akulembedwa maina kuti akalandire chakudya kapena ndalama ife mafumu osatengapo mbali ndiye mapeto ake, anthu osayenera kupindula nawo akupezeka pamndandanda, adatero Senior Chief Chapananga wa ku Chikwawa. +Mfumu yaikulu Chadza ya ku Lilongwe idati chifukwa choti anthu omwe akuchita kalemberayu sadziwa bwinobwino madera omwe akugwiramo ntchitowo, midzi yambiri ikudumphidwa kusiya anthu ambiri padzuwa. +Anthu omwe akuchita kalembera sadziwa malire kuti adayenda bwanji kapena kuti kuli anthu ochuluka bwanji. Pachifukwachi, midzi yambiri ikudumphidwa; mwachitsanzo, mdera langa lino, muli Senior Group Mwenda yemwe ali ndi mafumu 80 komanso anthu 6 000 omwe adumphidwa, adatero Chadza. +Senior Chief Lukwa wa ku Kasungu adati mwa mafumu opitirira 200 a mdera lake, mafumu 6 okha ndiwo alowa mukalembera wa anthu olandira chakudya kutanthauza kuti midzi yambiri yasiyidwa ndipo avutika. +Mfumu yaikulu Chindi ku Mzimba adati iye adangomva kuti anthu ena alembedwa maina ndipo kuti ena ayamba kulandira chakudya koma osadziwa komwe zikuchokera ndi momwe zikuyendera. +Adalembana okha komweko ife sizidatikhudze ayi komanso zoti anthu akulandira chakudya tikungomva. Mwachitsanzo, ndidangomva mphekesera kuti cha ku Edingeni anthu adalandirako chimanga koma ndilibe umboni, adatero Chindi. +Mneneri wa nthambi ya Dodma Jeremiah Mphande adati njira yomwe ikugwiritsidwa ntchito posankha anthu ndiyamakono komanso yothandiza kuchepetsa chinyengo ndi katangale yemwe adalipo kale. +Njirayi yomwe akuitcha Unified Beneficiary Registry (UBR) imatenga kaundula wa anthu ovutika nkuwayika mmagulu potengera mavutikidwe awo ndipo kuchoka apo amazindikira thandizo loyenera kupereka ku maguluwo. +Kuchoka pa mndandandawu, amthandizi pakhomo, amatengapo anthu awo, a ntchito za chitukuko amatengaponso ndipo ofunika thandizo la chakudya nawo amachoka momwemo. Njirayi imachepetsa kulakwitsa kowonjezera kapena kuchotsera anthu mu kaundula, adatero Mphande. +Malingana ndi DC wa mboma la Lilongwe, Charles Makanga, bomali lidatsatadi njira yatsopano pofuna kuthetsamavuto ena omwe adalipo mnjira yakale monga kulowetsa ndale za pamudzi mupologalamu. +Chomwe chimachitika mundondomeko yakale nchakuti mafumu amayenera kugwirira ntchito limodzi ndi makomiti monga Village Development Committee (VDC) ndi Area Development Committee (ADC) koma pamakhala kuyendana mmbali. +Tili ndi zitsanzo zambiri zomwe kumapezeka kuti mfumu payekha walemba maina kapena anyamata ena a mukomiti alemba maina kwa okha ndiye zimasokoneza pologalamu, adatero Makanga. +Akhalenso ndi moyo wautali Tsiku limenelo ndidakwiya zedi pa Wenela. Mkwiyo wanga udali waukulu zedi moti ndidafuna kuphulika. Inde, udali mkwiyo waukulu zedi moti kuchita chibwana nzimbe ndithu ikadamera pamsana! Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mminibasi imene ndinkaitanira nthawi imeneyo munkalira nyimbo ya King Yellowman, inde, mmodzi mwa oimba chamba cha dancehall kuchokera ku Jamaica. Mutu wa nyimboyo ndi Zungguzungguguzungguzeng. Amene sakuidziwa nyimbo imeneyi ngoyenera kudzidabwa chifukwa inetu ngakhale ndili kwathu kwa Kanduku, mawu ake ndinkawadziwa bwino: Zungguzungguguzungguzeng Zungguzungguguzungguzeng Seh if yuh have a paper, yuh must have a pen And if yuh have a start, yuh must have a end Seh five plus five, it equal to ten And if yuh have goat, yuh put dem in a pen And if yuh have a rooster, yuh must have a hen, now: Chidandikwiyitsa kwambiri chidali chakuti mminibasimo mudatsika munthu wachialubino. Mzibambo adabopha ulusi mochititsa kaso. Atatsika munthuyo, anthu adayamba kuliza malikhweru. Ena adali kukuwa: Mamiliyoni awo!!! Mawu amenewa ndiwo adandikwiyitsa zedi. Ndidagwira mmodzi mwa anthu amakuwawo. Ndidamulawitsa makofi. +Kupusa! Amene mukukuwa zopusazi ndinu oipa, chimodzimodzi amene amapha maalubino ati kuti akachite zizimba. Kulemera kwake kuti? Ndipo chuma chake chodyedwa ndi njenjete chomwechi? ndidafunsa mozaza. +Nditapita kumalo aja timakonda, ndidapeza akuvina nyimbo ya Kenneth Ninganga ndi Geoffrey Zigoma. Koma kudali dansi yotha malo. Ndipo mawu anthetemya a Zigoma adanditenga mtima osakhala masewera. +Mayo mayo, mayo mayo ndathera pano! Takondwera mwalowa mbanja aye. +Itatha nyimboyo, wapamalopo, Gervazzio, adatsegula wailesi kuti timvere nkhani. +Mwina nkumva kuti Moya Pete wanenapo chiyani za kubedwa, kuphedwa ndi kunyozedwa kwa maalubino, adatero. +Woweruza milandu wina walamula kuti munthu amene anaba munthu wachialubino wina akaseweze kundende zaka ziwiri, adali kutero wowerenga nkhani. +Abiti Patuma adakwiya. Mtima wake umachita kumveka kugunda ngati uphulika! Zaka ziwiri basi? Munthuyo amafuna akagulitse munthu wachialubinoyo kuti achotse ziwalo zina ati zizimba ndiye kungomupatsa zaka ziwiri kundende? Munthu wakuba ngombe akupatsidwa zaka 7 koma wakuba munthu mnzake kungopatsidwa zaka ziwiri basi? adazaza. +Nanenso mkwiyo udachititsa mwazi wanga kuthamanga. +Zilango amati zizichititsa ena kuti asayerekeze kupalamula. Chilango ngati ichi chingaopseze ena? Enatu akufukula mitembo ya maalubino ati zizimba. Ayi ndithu, ufiti wotere wafika povuta, ndidatero. +Mkwiyo wandizinga. Mtima wanga ukupweteka. Ndikumva kutentha ngati munthu wodya nsima yamoto, ndiwo zake khwanya wothiridwa tsabola wakambuzi wochuluka komanso atakhala padzuwa la 12 koloko masana. +Mmutu mwanga mudayamba kuyenda nyimbo ya Salif Keita. Ngati mu Africa muli anthu odziwa kuimba, Salif Keita ndi mmodzi mwa iwo. Ngakhale ndi wachialubino, Salif ali ndi luso ndipo amadziwika padziko lonse lapansi chifukwa cha nyimbo zake zogwira mtima. Ndimukumbuka bwino chifukwa tsiku lomwe adabwera ku Malawi ndidanyamula zikwama ndi magitala ake kulowera ku French Cultural Centre. +Nyimbo yake idali ya Folon, imene adaimba ndi wotchuka winanso, Youssour Ndor. +Koma abale nkhanza izi ziyenera kutha. Momwe ndikuonera mchitidwe wonyansawu udayamba kalekale. Ndikumbuka kalekale tinkauzidwa kuti ma alubino amangosowa, samwalira. Ndiye kuti nkhanzazi zidayamba kale. Anthu akuba anzawowa adayamba izi kalekale, adatero Abiti Patuma. +Achenjeza zobzala chinangwa cha matenda Katswiri oona za tizilombo toononga komanso toyambitsa matenda ku mbewu wa kunthambi ya kafukufuku ya Bvumbwe Research Station, Dr Donald Kachigamba, wati alimi apewe kubzala mbewu ya chinangwa chomwe chikuonetsa zizindikiro za matenda. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Pamene mvula ikugwa ndipo Madera ena imagwa mocheperako, alimi ena padakalipano ali pa kalikiliki kubzala mbewuyi kuti adzapeze chakudya ngakhalenso kugulitsa. +Kachigamba adati matenda a chinangwa omwe azunguza kwambiri mmaiko ambiri a mu Africa kuphatikizapo Malawi ndi a khate (cassava mosaic) komanso oola (cassava brown streak). +Matenda a khate amapangitsa masamba a chinangwa kukwinyana pomwe matenda a kuola amapangitsa mtengo wa chinangwa kuoneka okandikakandika komanso chinangwa chenichenicho chimaola mkati mwake, adatero katswiriyu. +Khate la chinangwa limachititsa masamba kukwinyika Iye adalangizanso kuti ngati mbewu zina zayamba kuonetsa zizindikirozi pamene zili mmunda, mlimi akuyenera kuzizula ndi kuzitaya zikadali zazingono kuti zisakhale gwero la matendawa ku mbewu zina. +Katswiriyu adaonjeza kuti kachilombo kotchedwa gulugufe oyera ndi komwe kamafalitsa matendawa mmunda wa chinangwa. +Gulugufeyu payekha sioopsa koma kuipa kwake ndi kwakuti amafalitsa matendawa mmunda wa chinangwa choncho chofunika ndi kungoonesetsa kuti mmunda mulibe matenda, adatero katswiriyu. +Mkulu oona za mbewu za gulu la chinangwa ndi mbatata kunthambiyo, Miswell Chitete, adati matendawa ndi ofunika kuwapewa chifukwa kupanda kutero, mlimi akhonza kupeza zokolola zochepa kwambiri. +Alimi akuyenera kupewa matenda a chinangwa chifukwa ena mwa matendawa, mwachitsanzo khate, limatha kupangitsa chinangwa kuti chisabereke nkomwe kotero mlimi akhonza kungotaya mphamvu zake pachabe, adatero mkuluyo. +Mphatso Jalasi, yemwe amachita bizinesi yolima ndi kugulitsa mbewu ya chinangwa mboma la Zomba wati matendawa akupangitsa kuti mbewu ya chinangwa ikhale yoperewera. Iye adati kuperewera kwa mbewuyi ndi komwe kunamupangitsa kuti ayambe kulima ndi kugulitsa mbewu ya chinangwa. +Iye adati akuvutika kuti achulukitse mbewu ya chinangwa yopirira ku matendawa chifukwa siichita bwino kuchigawo cha kummwera. +Ngakhale pali mbewu yopirira ku matendawa, mbewuyi ndiyosankha madera komanso ndi yowawa kotero pakufunika mbewu yosawawa komanso yosasankha Madera, adatero Jalasi. +TUM imemeza sitalaka ya aphunzitsi lolemba Makolo, katswiri apempha boma lichitepo kanthu Sukulu za boma za pulayimale ndi sekondale mdziko muno zikuyembekezereka kuima kuyambira mkucha Lolemba ngati aphunzitsi angayambedi sitalaka pofuna kukakamiza boma kuti liyankhe madandaulo awo. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Akufuna zawo: Aphunzitsi kunyanyala ntchito mmbuyomu Chikalata chomwe bungwe la aphunzitsi la Teachers Union of Malawi (TUM) lalembera boma ndi nthambi zosiyanasiyana chati aphunzitsi onse msukulu za boma za pulayimale ndi sekondale ayamba kunyanyala ntchito mkucha uno ngati boma silipereka yankho logwira mtima pa madandaulo omwe bungweli lidapereka kuboma. +Mtsogoleri wa bungwe la TUM Chauluka Muwake adati mwa madandaulowa, undunawu udangoperekako ndalama zokapumira kusiya mavuto enawo osayankhidwa mogwira mtima. +Bungwe la TUM lidapereka madandaulo 24 ku unduna wa zamaphunziro ndipo ena mwa iwo ndi kutsitsa aphunzitsi omwe adakwenzedwa pantchito; kulephera kuonjezera malipiro aphunzitsi omwe adakwenzedwa mchaka cha 2013; kulephera kulipira aphunzitsi a msukulu za sekondale ndalama zomwe amayenera kulandira pokapuma; komanso kulephera kulipira aphunzitsi a kupulayimale ndalama zamgonagona. +Nkhaniyi yakhudza makolo omwe ali ndi ana msukuluzi ndipo katswiri pa zamaphunziro, Benedicto Kondowe, wati nkhaniyi yafika apa kaamba ka kulephera kwa unduna wa zamaphunziro kupereka chilimbikitso kwa aphunzitsi. +Kondowe wati ngakhale malipiro a aphunzitsi ali ochepa, boma litamawalipira munthawi yake ndi kuwapangira zinthu zina zingonozingono moyenera, aphunzitsiwa akhoza kukhala ndi chilimbikitso pantchito yawo. +Iye adati ndondomeko ya maphunziro mdziko muno ndi yothinana mwakuti kuimitsa maphunziro ndi sabata imodzi kapena ziwiri ndi nkhani yoopsa kwambiri pamaphunziro kwa makolo, ophunzira ndi aphunzitsi. +Choyamba, kukakhala sitalaka, sukulu zambiri zimabweza ana kuopa zipolowe. Pamenepa muganizire makolo kumbali ya ndalama zoyendera ndi zina zomwe adali atagula kale. +Kwa ana, nchosokoneza kuyamba kuwaphunzitsa kenako aime chifukwa ena amavutika kutolera zinthu msanga. Kwa mphunzitsi, ntchito yomwe akadapanga pasabata ziwiri ndi yambiri ndiye pofuna kuti agwirane ndi ndondomko, amaphunzitsa mongowaula ana bola amalize, adatero Kondowe. +Lameck Majawa, kholo lomwe lidalankhula ndi Tamvani Lachiwiri bungwe la TUM litatsimikiza za sitalakayi, adati boma likadagonjera aphunzitsi nkuwapatsa zofuna zawo kuti sitalakayi isachitike ndipo mavuto omwe angadze ndi sitalakayi apeweke. +Iye adati maphunziro akulowabe pansi chifukwa ngakhale popanga ndondomeko ya chuma cha dziko lino unduna wa zamaphunziro umaganiziridwa ngati umodzi mwa maunduna omwe amapatsidwa ndalama zambiri. +Izi si zoona, ayi, nthawi ndi nthawi tizimva nkhani imodzimodzi popanda kupanga njira zothetsera mavuto amenewa? Tatopa nazo izi, aganizepo bwino ndi kupangapo kanthu kuti sitalakayi isachitike, adatero Majawa. +Kholo lina, Grace Chawinga, adagwirizana ndi Majawa kuti njira ndi imodzi yokhayo yopereka zomwe aphunzitsi akufuna boma liwachitire kusiyana nkumakokanakokana, zomwe adati nkuphwanya ufulu wa ana olandira maphunziro apamwamba. +TUM yapereka kalata yake ku ofesi ya mlembi wamkulu wa boma, mlembi wa nthambi yopereka ndalama za boma, mlembi wa unduna wa zantchito, kubungwe la Maneb, nthambi yoyanganira ntchito ya uphunzitsi, likulu la mabungwe a anthu apantchito ndi kumaofesi oyanganira za maphunziro mmaboma. +Mkalatayi, TUM yati aphunzitsi onse msukulu za boma za sekondale ndi pulayimale ayamba kunyanyala ntchito Lolemba ngati boma silipereka yankho logwira mtima pa madandaulo omwe bungweli lidapereka kuboma. +Mneneri wa unduna wa zamaphunziro Manfred Ndovie adauza nyuzipepala ya The Nation kuti undunawu sungakwanitse kuthana ndi zonse zomwe aphunzitsiwa akufuna koma pangonopangono. +Adanena izi zokambirana zomwe zidaliko pakati pa bungwe la TUM ndi nthumwi za boma kuyambira Lachinayi sabata yatha zisadachitike ndipo pamapeto pa zokambiranazo, TUM idati boma silidawayankhe momveka bwino ndipo pachifukwachi sitalaka ikhalapo baso. +Zokambiranazi zitatha, Muwake adauza nyuzipepala ya The Nation kuti boma lili ndi ndalama za aphunzitsi zokwana K1.4 biliyoni zoyanganirira mayeso a MSCE omwe sadatuluke; K246 miliyoni za aphunzitsi omwe adakwenzedwa koma samalandira molingana ndi giredi yawo; komanso K103 miliyoni za aphunzitsi opuma ndi omwe adamwalira. +Kondowe adati ngakhale nkhaniyi ndi yobwezeretsa maphunziro mmbuyo, aphunzitsi ali ndi mfundo zokwanira zochitira sitalaka kaamba koti nthawi zambiri boma siliika chidwi pa mavuto awo. +Pachiyambi, TUM idakonza zoyamba sitalaka Lolemba lathali tsiku lotsegulira sukulu koma zidalephereka chifukwa aphunzitsi adati adali asadalandire chidziwitso chenicheni ndipo sukulu zambiri aphunzitsi adaphunzitsa. +Lamulo latsopano la zipani alikambirana Dziko lino lili ndi zipani zoposa 40. Komatu mwa zipanizi zisanu zokha ndi zomwe zimakangalika pomwe zina zili ziii ngati madzi a mfiliji kudikira nthawi ya zisankho. Komatu mchitidwewu ukhala mbiri yakale malinga ndi lamulo latsopano la zipani lomwe aphungu a Nyumba ya Malamulo akuyembekezera kukambirana akakumananso mwezi wa May. +Malinga ndi mtsogoleri wa Nyumba ya Malamulo, Kondwani Nankhumwa, aphungu adzakambirana za lamuloli mwezi wa May chifukwa pamene aphungu akukumana panopa, nthawi ndi yochepa. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kupereka ndalama, zinthu zina kwa ovota kudzaletsedwa Tikadakonda tikadakambirana za lamuloli koma nthawi yangochita njiru. Imeneyi ilowanso pamndandanda wa zokambirana za mwezi wa May, adatero Nankhumwa. +Ndi lamuloli, zipani zizikakamizika kuonetsa kuti zikugwira ntchito yake, monga kupanga nawo zisankho, komanso kupanga misonkhano yaikulu ya mamembala mchipani ndi cholinga choonetsa kuti zikugwiradi ntchito zotumikira anthu. +Zikapanda kukwaniritsa izi, mpamene mkulu woyanganira zipani azizichotsa mkaundula. +Lamulo latsopanolo lidzachotsa lamulo lakale la zipani lomwe limaona kulembetsa kwa chipani ndi ndondomeko zotsatira. +Mwa zina, lamulo latsopanolo lomwe lili ndi magawo 8 likuunikira zingapo, monga kukhazikitsa ofesi ya wolembetsa ndi kuthetsa zipani, zipani kulongosola bwino momwe zimapezera ndalama komanso kuti mamembala azidziwa momwe ndalama za chipani zikuyendera. +Lamulolo likutambasulanso za kayendetsedwe ka zisankho monga kuthana ndi mchitidwe wopereka ndalama ndi zinthu zina kwa ovota nthawi ya chisankho komanso kukhala membala wa zipani zingapo. +Polankhulapo za kufunika kwa lamuloli, mkulu wa bungwe limene muli zipani zosiyanasiyana la Centre for Multiparty Democracy (CMD), Kizito Tenthani adati adati padakalipano mamembala a zipani alibe mphamvu zenizeni mzipani mwawo, zimene lamulolo likufuna kusintha. +Bungwelo ndi lomwe lakhala likukambirana ndi mbali zonse zokhudzidwa momwe lamulolo lidzathandizire zipani kukwaniritsa ntchito yoimirira anthu komanso kupereka umwini wa chipani kwa mamembala. +Zimaoneka ngati atsogoleri ndi amene amakhala ndi mphamvu zambiri mchipani. Lamololi lithandiza kusintha zimenezi. Kuonjezera apo, ndale zathu Mmalawi muno zakhala kwambiri zodalira ndalama. Panthawi ya chisankho, zipani, komanso amene akufuna kuimira zipani pamipando yosiyanasiyana amakhala akupereka ndalama ndi zinthu zina ncholinga chokopa anthu kuti awavotere, adatero Tenthani. +Iye adati mchitidwewu umapangitsa ndale kukhala zodula, komanso anthu omwe ali ndi ndalama kukhala ndi mwayi wolowa mmaudindo ngakhale nthawi zina anthu oterowo amakhala opanda masomphenya a mmene angathandizire anthu kudera kwawo. +Lamuloli lithandiza kuthetsa mchitidwe umenewu. Likufunanso zipani zandale zizinena komwe zimapeza ndalama ncholinga chothetsa mchitidwe wa katangale, adaonjezera Tenthani. +Koma mmodzi mwa akadaulo pa ndale mdziko muno Rafiq Hajat adati palibe chaphindu chomwe lamulo latsopanolo liphule chifukwa lamulo lomwe lilipo lakanika kugwiritsidwa ntchito bwino. +Hajat adati mwachitsanzo lamulo lakaleli limati chipani chilichonse chizipereka kwa mkulu wakalembera wa zipani momwe achitira pa chuma chaka chikamatha ndipo kuti ngati satero chipanicho chizithetsedwa. +Komatu izi sizili choncho. Ngati tikukanika kukwaniritsa zinthu ngati izi, ndiye lamulo latsopanoli tidzaligwiritsa ntchito bwanji? adadabwa Hajat. +Iye adati aphungu ayenera kutenga nthawi yaitali kukambirana zinthu monga za kuba ndalama mboma (cashgate), njala ndi zina osati za lamulo la zipanili. +Tiyeni tiyangane njira zogwiritsa ntchito lamulo lakale lomweli, adatero Hajat. +Komatu Tenthani adatsutsa izi polongosola kuti lamuloli ndi losiyana kwambiri ndi lakaleli chifukwa layesera kukonza zimenezi ndipo akukhulupilira kuti lidzagwiritsidwa ntchito bwino. +Choti anthu adziwe nchakuti lamulo lilipo pano lidapangidwa mwachangu kwambiri ncholinga choti mchaka cha 1993 anthu athe kulembetsa zipani kuti zikapange nawo chisankho cha 1994. Mmalo ambiri, lamulo lili panoli silinaunike bwino maka pankhani ya kayendetsedwe ka zipani, komanso kuumiriza kuti zipanizo zitsatire malamulowo, adalongosola Tenthani. +Mudali mu basi ya National Shamuda Drake ndi mtolankhani wa wailesi ya Galaxy yemwe tsopano ali pabanja ndi mkazi wake Madalitso Moyo. Momwe Drake amayamba ulendo wake wochokera ku Lilongwe komwe amakaona mchimwene wake kupolisi ya Kawale, sadadziwe kuti nkupeza nthiti yakeyo. +Naye Madalitso, pamene amachoka ku Dwangwa komwe amagwira ntchito kukampani yopanga shuga ya Illovo ulendo wa ku Mzuzu kukaona abale patsiku lokumbukira anthu amene adafera ufulu wa dziko lino pa 3 March, samadziwa kuti nkupeza wachikondi. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Drake ndi Mada adamangitsa ukwati ku Mzuzu Awiriwa adakhala mpando woyandikana mubasi ya National Bus Company koma sanayankhulitsane, kufikira pamene adafika pamalo ochita chipikisheni apolisi a Matete. +Apa mpamene tidayamba kulankhulana ndipo adandifotokozera komwe amalowera. Macheza adapitirira ndipo titafika pa Bandawe, ndidamufunsa ngati angandipatse nambala yake ya foni yomwe adandipatsa ndikutsika basi pasiteji ya kwathu ku Malaza ku Chintheche, adafotokoza Drake. +Drake adamuimbira foni usiku omwewo kuti amve wayenda bwanji koma sadakambe zambiri. +Drake adati patadutsa masiku angapo, adamuyimbiranso kumpatsa moni, apa adali njoleyo idali itabwerera ku Dwangwa ndipo adayankhulitsana ngati ongodziwana chabe. +Koma nditakhala masiku angapo, mtima wanga udayamba kukankha mwazi ndipo ndidamuyimbira kuti ndikadakonda titakumana bwino ndi kukambirana nkhani ina. Iye adati adalibe mpata chifukwa ntchito yawo amagwira sabata yonse, koma nditalimbikira adangoti ndidzapite nthawi ya nkhomaliro ndipo tidzakambirana kwa mphindi 30 zokha,adatero Drake. +Ndipo tsikuli litakwana Drake adakampezadi Mada akadali kuntchito ndipo atakumana adamtengera kunyumba kwake komwe kudalinso anzake ena awiri. Apa adamkonzera chakudya ndipo adakambirana uku akudya. +Adandifunsira banja, ndipo ndidamuuza kuti ndikaganize kaye, adatero Mada. +Patatha masiku atatu, Drake adakokanso chingwe ndipo cimwemwe chidadzala tsaya Mada atanena kuti walola. +Abusa mayi Agness Nyirenda ndiwo adamangitsa ukwati ku Zolozolo CCAP mumzinda wa Mzuzu ndipo madyerero adali kusukulu ya sekondale ya Katoto. +Afisi a ku ntcheu abwereranso? MAyi adaphedwa, ana ake anayi ndi mlamu wake adavulazidwa. Pano ziweto 10 zagwidwa mmidzi 14 ya mwa T/A Phambala mboma la Ntcheu. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Alenje aboma amene adapitako kukasaka afisiwa, adangokhalako masiku atatu ndi kuchokako, lero anthu agwidwa ndi mantha. +Mkulu woona nyama za kuthengo ndi nkhalango Bright Kumchedwa adati nkhaniyi adaimva ndipo lipoti la momwe alenjewo adayendera lidatumizidwa. +Harrison Lano, mmodzi mwa olumidwa ndi fisi mchipatala Tikukonza zoti tibwererenso kumudziko. Chomwe tikuyangana panopa ndi ndalama. Zonse zikatheka, tibwerera konko, adatero Kumchedwa. +Koma iye adati anthu aleke kuyenda usiku komanso asalole kuti ana aziyenda okha kuopa ngozi. +Kodi afisi a ku Ntcheu amene adatchuka mzaka za mma 1990 ayambiranso? Ili ndiye funso la anthu a mbomali. +Bambo wa ana ovulazidwawa akuti moyo wawo uli pachiswe ndipo boma likuyenera lichite kanthu kupulumutsa anthuwa. +Bamboyu, Alfred Thala, wa mmudzi mwa Thala akuti chivulazireni ana ake ndi kupha mkazi wake, anthu akukhala mobisala. +Pano akumayenda mmagulu, tsiku lililonse afisi akumamveka akulira kuyambira cha mma 5. Tili ndi mantha kuti tsiku lililonse tingaonenso ngozi ngati yomwe idachitika, adatero Thala. +Iye adati chiphereni mkazi wake pa 2 December chaka chino, mudzi wawo mwagwidwa ziweto 6. +Sabata yatha yomweyi adzagwira nkhumba kunyumba kwanga. Mbuzi agwira mwa anthu ena mmudzi momwemu. Komanso mudzi woyandikana ndi ife agwira mbuzi zinayi. +Akumafika pakhomo, sungatulukenso kuopa kuti akugwira, uwu ndiye ukumakhala mwayi wawo kuti agwire ziweto, adatero Thala. +Ngoziyo itachitika, alenje a boma adafikako koma adangokhala masiku atatu nkuchokako zomwe sizidakomere anthu akumeneko. +Tsiku lililonse afisi amadutsa koma sadaphe ngakhale fisi mmodzi mpaka adapita. Tidawauza kuti asachoke koma sadamvere ndipo adapita, adatero Thala. +DC wa boma la Ntcheu Paul Kalilombe adati nkhaniyi adaimvanso moti panopa akukambirana ndi oyanganira za nkhalango ndi nyama zakuthengo kuti athandize. +Nkhani yoti afisi avuta kuno tidaimva ndipo tikulumikizana ndi alenje kuti atithandize, adatero Kalilombe. +Koma Senior Chief Kwataine ya mbomali yati ngakhale afisiwa avuta, anthu asaganize kuti afisi amene adatchuka padzana abwereranso. +Afisi a nthawi imene ija adali odabwitsa chifukwa amayenda masana. Amakhoza kufika pamaliro nkugwira munthu. Amene aja adapita chifukwa zimaonetsa kuti akuchokera ku Mozambique. Afisi awawa kulipo akuchoka, adatero Kwataine. +Komabe Thala akupenekera kuti alipo akufuna kuwachita chipongwe anthu a midzi yawo. +Alenje amatchera mfuti, amaikapo nyama kuti adye, upeza angodya nyama inayo koma nyama yomwe yayandikira kotulukira zipolopolo samadya. Awa ndi afisi enieni? Ndikukaikira. +Afisi enieni amathawa anthu komanso amayenda usiku wokhawokha dzuwa likalowa, koma awawa akudabwitsa chifukwa akuyenda masana, adaonjeza. +Basi ayisempha Tsiku limenelo sitidakhale pa Wenela. Palibe ojiya, osolola, osenza ndi oitanira amene adatsala pa Wenela. +Tidakwera galimoto la mkulu wina kulowera ku Lilongwe. Si kuti timapita kuja kulikulu la boma kumene masamu ogula mmera asokonekera. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Sindingakambe nkhani imeneyo chifukwa tonse tikudziwa kuti lingaliro la Dizilo Petulo Palibe, malinga ndi kufotokoza kwa Joloji Chiponda, lidali logula chimangacho ku Brazil. Zoona mpaka kuoda chimanga ku Brazil! Nkhani ya chimangayi kwa ine ndiyongotaya nthawi. Ngati Moya Pete adalamula asilikali ake kukwidzinga uja wogina ndi amayi oposa 100 bwanji akulephera kulamulanso amene akuganiziridwa kukazinga mmera wa tonse pano pa Wenela? Zosamveka konse kuti mzimayi woti akufuna kugula chimanga choti adye pakhomo pake, mmalo mopita yekha kumsikako kutuma wina kuti akamugulire kenako nkumadandaula kuti waberedwa! Abale anzanga, tingoyerekeza kuti mwalemba wantchito, ndiye mukumukaikira kuti anaba ndiwo. Kenako mukuuza akazi kapena amuna anu kuti afufuze momwe anabera ndiwozo, wantchito wanu akapita pachulu nkumakuwa kuti: Sindinabe ine! Sindinabe! Chomwe ndimadabwa pano pa Wenela nchakuti nchifukwa chiyani aliyense amafuna kutalika zala pankhani za chimanga? Tidamvapo kuti Adona Hilida adagulitsa matani ochuluka kupita nawo ku Kenya. Nanga za Thursday Jumbo uja naye adadyapo zake za chimanga. Za makuponi ndiye ndisachite kunena. +Nsataye nazo nthawi izo. +Chaka chino talowa Talowa ndi adani omwe Akufuna moyo wanga Kuti aononge Chauta thandizeni Iyi ndi nyimbo imene tinkamvera mugalimoto ya mkulu amene adatitenga. Tidafika kubwalo la mpira latsopano kumene zipolopolo ndi nyerere zimamenyana. Inu, munthu nkupha nyerere poyiwombera! Ndidangomva kuti ena adathyola mipando, kutenga makalilole ndi zina zotero! Komanso abambo ena ankalowa kuzimbudzi za akazi! Utatha mpira, sindikudziwa kuti udatha bwanji, Abiti Patuma adandikoka kuti timuthawe mkulu uja. +Tidakakwera basi imene sindikuyidziwa bwino. Mudali anyamata a Chimwemwe kwambiri. Iwo amangoti 5 kwa 1, 5 kwa 1. Onse atamuona Abiti Patuma adakuwira limodzi: Abiti Patuma! Yo-yo-yo! Wina adamukumbatira, wina kumupsopsona patsaya. +Osadanda, mwayiphula basi! Ndikuthangatani nonse mbasi momwe muno, adatero Abiti Patuma. +Koma abale! Kudalitu kulandirana! Basi imamveka ndithu kuti mashoko siali bwino komabe mmodzimmodzi adali kulandira chithandizo kuchokera kwa Abiti Patuma. +Adati tinyamuke, ulendo wobwerera pa Wenela. +Tili mnjira, yemwe amaoneka kuti ndi mkulu wa anyamatawo adati: Tikakafika ku Mwanza, tikadzera kwa Ayaya tikayamike chifukwa watithandiza kupeza basi. +Ulendo wa kwa Ayaya sunatheke chifukwa basi idatchona pa Manjawira. Poyamba tinkadya kanyenya kuti mwina iyenda. Kenako kudali kusaka mango, ngumbi ndi zina mpaka mdima udagwa. +Siteshoni ya Nkaya ifewetsa maulendo Gawo lachiwiri lomanga siteshoni ya sitima ya Nkaya mboma la Balaka layamba ndipo ntchitoyi ikuyembekezeka kutha mu November chaka chino. +Mneneri wa bungwe loona sitima zapamtunda la Central East African Railways (CEAR) Chisomo Mwamadi wati gawoli likatha, anthu amene amagwiritsira ntchito sitima zapamtunda athandizika chifukwa sitima zizinyamula katundu wambiri komanso ziziyenda mwachangu. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mwamadi: Samalani njanji Mu June chaka chino, bungweli lidamaliza gawo loyamba lomwe kudali kumanga njanji zinayi kuti sitima zapamtunda zizidutsana pamalopa. +Gawo lachiwiri lidayamba litangotha gawo loyamba lomwe kukhale kumanga njanji ina yotalika ndi makilomita awiri komanso kumanga njanji zinayi zomwe zizithandiza kusungirako sitima komanso kumasula mabogi. +Njanji zimenezi ndizomwe tizimasulira sitima ngati ili ndi vuto komanso kusungirako sitima. Pamene tikupanga izi, sitima zina zizitha kumayenda mopanda kusokonezedwa. Izi sizimachitika poyamba chifukwa tidalibe malo, koma tsopano izi ziyamba kuchitika popanda vuto lililonse, adatero Mwamadi. +Padakali pano, malo amene amangepo njanjizi asalazidwa kale komanso katundu wafika kuti ntchitoyi iyambe tsiku lililonse. +Njanji yopita ku Nkaya ndi imeneyi Mwamadi akuti gawoli likatha, anthu amene amagwiritsira ntchito sitima asangalala kwambiri komanso bizinesi izichitika mwachangu. +Zonse zikatha, ndiye kuti Nkaya akhala malo akulu pomwe sitima zizisemphana komanso kumamangirira mabogi. Sitima yochokera ku Mwanza, Blantyre, Liwonde komanso Kanengo zizidutsana pa Nkaya komanso titha kumamanga mabogi. +Chawomola chipande: Mwa anthu 133 345 olembetsa 25 150 okha avota Kwatsala utsi wokha, nsima yapsa, chapakula chipande ndipo pakula mtanda pagwera chipani cha MCP chomwe chateteza mpando wa phungu wa kumadzulo kwa boma la Mchinji ndi kupata makhansala awiri mchisankho chachibwereza chomwe changothachi. +Lachiwiri lapitali, zipani zinayi mwa zipani 50 zomwe zili mdziko muno zimalimbirana mpando wa phunguwu ndi makhansala anayi a mmawodi a Kaliyeka ku Lilongwe, Bunda ku Kasungu, Bembeke ku Dedza ndi Sadzi ku Zomba potsatira imfa za omwe adali mmipandoyi. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ansah (C): Tichita kauni wamphamvu Powomola zonse Lachitatu, chipani cha MCP chidateteza mpando wa phungu ku Mchinjiko kudzanso kulanda mpando wa khansala wa Kaliyeka womwe udali mmanja mwa chipani cholamula cha DPP ndi mpando wa khansala ku Bembeke womwe udali mmanja mwa woima payekha. +Mwachaje satafuna. Nacho Chipani cha DPP sichidabwereko chabe chifukwa chidapambana mipando ya makhansala mmadera a Sadzi komanso Bunda pomwe zipani za PP ndi UDF sizidaphule kanthu pazisankho zachibwerezazi mmadera onsewa. +Menyani: Zaonetsa kuti MCP ndi chipani champhamvu Ngakhale anthu osiyanasiyana ayamikira momwe zisankhozi zayendera, bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) ndi akatswiri ena ati kuchepa kwa anthu omwe adaponya voti ndi utsi wofunika kuunika pomwe ukuchokera. +Mwa anthu 133 345 omwe amayembekezeka kuponya voti, anthu 25 150 okha ndiwo adavota mmadera onse asanu ndipo wapampando wa bungwe la MEC, Jane Ansah, adati izi nzofunika kauni wamphamvu. +Tikuyenera kubwerera kwa Amalawi kukawafunsa pomwe pali vuto kuti asamabwere mwaunyinji kudzavota ngati momwe amabwerera kumisonkhano ya kampeni, adatero Ansah. +Kasaila: DPP idachitabe chamuna Katswiri wa zandale kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College, Boniface Dulani, adati gwelo la vutoli ndi khalidwe la andale omwe amaonetsa chibale nthawi ya kampeni nkusintha mawanga zikawayendera. +Anthutu amafuna zotsatira osangoti kankheni kenako mukakwera mmwamba ubale watha. Pokhapokha khalidwe lotereli litasintha, vuto lothawa kuvota silingathe, adatero Dulani. +Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe okhudzidwa ndi zisankho wa Malawi Electoral Support Network (Mesn), Steve Duwa, adati ichi nchizindikiro choti anthu adataya chidwi ndi zisankho. +Iye adati palibe chomwe chingalimbikitse anthu kukaponya voti pomwe nthawi ndi nthawi amakhumudwitsidwa ndi atsogoleri omwe adawasankha, makamaka pakayendetsedwe ka zinthu. +Ndanga: Izi zadutsa tiyangane zakutsogolo Vuto lalikulu nkusaganizira anthu omwe amaponya voti. Anthuwa amakhala ndi zambiri zochita koma amalolera kuzisiya kuti akaponye voti ndi chiyembekezo choti atumikiridwa bwino, ndiye zikapanda kuyenda momwe amayembekezera, zotsatira zake zimakhala zimenezi, adatero Duwa. +Mfundozi zidagwirizana ndi zomwe Tamvani wapeza kuchokera kwa anthu osiyanasiyana omwe akuti adatopa nkuika anthu mmpipando koma mapeto ake nkulandira chipongwe. +Tikaunika bwinobwino, timaona kuti zomwe timauzidwa pakampeni si zomwe timaona zisankho zikapita ndiye pena pake munthu umalingalira kuti bola nthawi yako uigwiritse ntchito ina, adatero Adam Potani, wochokera kwa Kaliyeka. +Naye Maria Silungwe wa ku Nchezi ku Lilongwe, adali ndi ndemanga yomweyo koma iye adawonjezera kuti andale ena akasankhidwa amafuna kuti anthu omwe adawasankhawo ndiwo aziwatumikira mmalo moti iwo ndiwo azitumikira anthuwo. +Chisankho chisadachitike, Tamvani adacheza ndi zipani zonse zomwe zimapikisana nawo ndipo zotsatira zidasonyeza kuti chipani chilichonse chidali ndi chiyembekezo chotenga mipando yonse. +Chitatha chisankho, tidafunsanso ndemanga za zipanizi ndipo kudaoneka kuti zotsatirazi sizidasinthe maganizo a zipanizi pa za tsogolo lawo. +Mneneri wa chipani cha MCP, Alekeni Menyani, adati zotsatirazi zidasonyeza kuti chipanichi nchamphamvu chifukwa chidatenga mipando yambiri ngakhale kuti chimapikisana ndi chipani cholamula pambali pa zipani zina. +Iye adati chisankhochi chidali ngati liwiro la mumchenga loyamba mosiyana chifukwa ena adali ndi mpata wogwiritsa ntchito zipangizo za boma nthawi ya kampeni pomwe zina amadalira mthumba mwawo. +Mneneri wa chipani cha DPP, Francis Kasaira, adati chipanichi chidachita chamuna chifukwa chidapita kumpikisanowu chitataya makhansala ake awiri ndipo chidakwanitsa kupezanso makhansala ena awiri kutanthauza kuti mphamvu sizidasinthe. +Ken Ndanga wa chipani cha UDF adati madzi apita ndipo kwatsala tsopano nkuunika pomwe chipanichi chidafooka kuti zomwe zachitika ulendo uno sizadzachitikenso mtsogolo. +Tidayesetsa kuti amve maganizo a chipani cha PP koma wogwirizira mpando wa mtsogoleri wa chipanichi, Uladi Mussa, sadayankhe foni yake yammanja maulendo angapo. +Ngati sipangaonekenso ngozi ina kapena wina kutula pansi udindo wake, ndiye kuti chisankho china chidzakhalako mchaka cha 2019 pomwe Amalawi adzasankhe mtsogoleri wa dziko, aphungu a Nyumba ya Malamulo komanso makhansala. +40 awaganizira kugwa mndenge yamatsenga Anthu 40 mboma la Ntchisi akuwaganizira kuti adagwa mndege yamatsenga yomwe anthuwo adakwera akuchokera kotamba. +Nkhaniyi idadzidzimutsa anthu ambiri okhala mmudzi mwa Chikuta mdera la mfumu yaikulu Chilooko mbomali Lachitatu pa 17 August pomwe chinthu china chachilendo, chomwe akuchiganizira kuti ndi ndege ya ufiti, chidagwa mmudzimo. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Phiri: Nayi ndenge ya matsenga Malingana ndi singanga Pilirani Phiri wa mmudzi mwa Ziwanda mdera la tidaitenga pamodzi ndi amfumu a mmudzimo nkupita nayo kupolisi ya Kamsonga komwe ndipo apolisi adatiuza kuti, ngati singanga, ine ndi amene ndingathe kuononga ndegeyo ndipodi ndidakaonongadi poitentha, adatero Phiri. +Titamfunsa kuti adadziwa bwanji kuti mndegemo mudali anthu 40, Phiri adati adaunika ndi galasi lake lomwe amaonera zamatsenga ndipo onse amene adali mmenemo akuwadziwa ndipo achikhala kuti boma limavomereza bwenzi akuluakuluwo atawatumizira nuclear kuti akhaule chifukwa akumaphunzitsa ana ufiti koma ndikatero ndiye kuti ndiika miyoyo ya makolo a anawo pachiopsezo chifukwa abale a mfitizo akhoza kukawachita chipongwe. +Ngakhale ena akuti ufiti kulibe, kunja kuno kukuchitika zoopsa ndipo zimatengera singanga amene adazama kuti adziwe zomwe zikuchitika, adatero singangayo. +Mkulu wa polisi pa Kamsonga Police Unit, Inspector Kennedy Kwalira, adatsimikiza za nkhaniyi. +Iye adati nkhaniyi adailandiladi ndipo ngati apolisi sakanatha kutengapo gawo pankhaniyo koma kuuza singangayo kuti ndi amene adakatha kuononga ndegeyo chifukwa malamulo a dziko lino savomereza kuti kunja kuno kuli ufiti. +Anatchezera Za chikondi ndi chibwenzi Agogo, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kodi chibwenzi ndi chikondi ndi zosiyana bwanji? Mwina funso limeneli likhoza kuoneka ngati lopanda nzeru koma kwa ine ndi lofunika kwambiri. Funso lina ndi loti kodi ngati mwamuna amakonda kulonjeza chibwenzi kapena wachikondi kuti adzakwatirana chonsecho mkazi samamulonjeza mwamuna wake, ndiye pamenepa mwamuna angathe kupitiriza chibwenzi kapena angomusiya? LF, Area 12, Lilongwe Wokondeka LF, Munthu utha kukhala ndi abwenzi ambirimbiri koma wachikondi mmodzi. Nthawi zambiri anthu satha kusiyanitsa pakati pa chikondi ndi chibwenzi. Chikondi ndi chozama kuposa chibwenzi; chikondi chimachoka pansi pa mtima ndipo nthawi zambiri anthu awiri akakondana maka pakati pa mwamuna ndi mkazi amagwirizana mzambiri moti nchifukwa chake mapeto ake amalolerana ndi kulumbira kuti adzakhala limodzi mpaka moyo wawo wonse mbanja, pamene chibwenzi mumatha kugwirizana pa zina koma kusiyana mzambiri zochitika. Nchifukwa chake munthu utha kukhala ndi abwenzi ambiri ngakhale uli pabanja, monga ndanena kale, koma amene umatherana naye nkhazi zakukhosi ndi zakumphasa ndi mmodzi yekha, wachikondi wako. Funso lako lachiwiri yankho ndi loti pachikhalidwe chathu mwamuna ndiye amafunsira mkazi ndipo ndi iyeyo amene amauza mkazi za cholinga chake pachibwenzi chawocho. Akazi ambiri amakhala ndi manyazi kunena kuti alola chibwenzi chonsecho mkati mwa mtima wawo alola kale. Ndiye munthu wamwamuna uyenera kumvetsa ndi kufatsa; osapupuluma chifukwa ukhoza kutsekereza mafulufute kuuna poganiza kuti mkazi sakunena chilichonse. Pamene pali chikondi sipasowa, zochitika zimasonyeza zokha kuti apa pali chikondi ngakhale wina asanene. +Amandikonda koma ine ayi Ndili ndi mwamuna amene akufuna akaonekere kwathu koma sindimamukonda kwambiri ngakhale kuti iyeyo amandikonda kwambiri. Ndiye akuti andikwatira zaka zinayi zikubwerazo. Pano ndakumana ndi wina koma akuti andikwatira zaka ziwiri zikubwera kutsogolo. Ndiye nditani, agogo? LC, Area 49, Lilongwe Zikomo LC, Mwana wanga, chimene ukufuna sindikuchidziwa. Iwe ukufuna kukwatiwa ndi mwamuna wotani? Wokukonda kapena amene akufuna ukwati pompanopompano ngakhale sakukonda? Vuto ndi chiyani ndi mwamuna amene ukuti amakukonda ndipo akufuna kudzamanga nawe banja zaka zinayi zikubwerazi? Nchifukwa chiyani udamulola poyamba ngati sumamukonda? Ndiye pano ukuti wapeza mwamuna wina amene akuti akukwatira zaka ziwiri zikubwerazi, makamaka ukufuna kuti ndikhuthandize chiyani pankhani imeneyi? Zonse zili ndi iwe mwini, koma chomwe ndingakulangize ndi choti si amuna onse amene amakhala ndi chikondi chenicheni. Wina atha kunena kuti tikwatirane lero ndi lero, koma mumtima mwake mulibe chikondi, pomwe wina anena kuti tikhale pachibwenzi zaka zinayi kenako tidzakwatirane pazifukwa zina ndi zina. Pa Chichewa pali mawu oti lero ndi lero linadetsa mnthengu, komanso ukasauka sunga khosi mkanda woyera udzavala. Enanso amati kuona maso a nkhono nkudekha. Mawu onsewa akutiphunzitsa kuchita zinthu mofatsa kuti tione ubwino patsogolo, osati kuchita zinthu mwakhamanikhani. Tsono monga ndanena kale, zili ndi iwe mwini chifukwa ukudziwa chomwe ukufuna. Koma ndikanakhala ndili ine, ndikanamupatsa mpata mwamuna woti waonetsa chikondi chenicheni kwa ine ngakhale anene kuti atenga nthawi kuti andikwatire. Chikondi chenicheni sichimaona nthawitu paja. +Kaneneni akakuchitikirani nkhanza, apolisi auza ana Pamene dziko lino limakumbukira masiku 16 othana ndi nkhanza za mbanja, apolisi amema atsikana kuti azikanena akachitidwa nkhanza kwa makolo awo kapena kupolisi. +Mkulu woyanganira zapolisi ya mmudzi mdziko muno, Yunus Lambat, adanena izi pokumbukira maikuwa, amene adayambira pa 25 November mpaka pa 10 December kusukulu ya Blantyre Girls. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Patsikulo, apolisi komanso akuluakulu a makampani osiyana adapita kukapereka uphungu komanso kuthokoza atsikana amene adakhoza bwino mkalasi. +Tadala: Nkhanza zisatilepheretse Mtsikana amene adasangalatsa anthu patsikuli ndi Tadala Kadzakalowa wa zaka 11 amene adakhala nambala wani musitandede 8. +Tadala, yemwe akukhumbira atadzagwira ntchito ya udotolo, adaponderera ophunzira 140 mkalasi mwawo. +Polankhula za tsikuli, Tadala adati iye ndi wokondwa kuti akuluakulu adapeza chabwino kuwafotokozera ufulu wawo komanso zomwe angachite ngati ufulu wawo waphwanyidwa. +Ndimafuna kudzakhala dotolo, izi sizingatheke ngati wina akupondereza ufulu wanga. Ndadziwa ufulu wanga, komanso zomwe ndingachite ngati wina atandiphwanyira ufuluwo, adatero iye. +Iye adalangiza atsikana anzake kuti asiye kumwa mowa ponena kuti izi zingasokoneze tsogolo lawo. +Akhumudwa ndi kutsika kwa nandolo Alimi a nandolo ena mboma la Mulanje, ati ali ndi nkhawa ndi kutsika mtengo kwa nandolo modzidzimutsa pamsika zomwe zikukayikitsa alimiwo ngati apindule naye chaka chino. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mmodzi mwa alimiwo, Henry Kapalasa, wa mmudzi mwa Chabwera kwa T/A Mabuka mbomalo, adati nandolo watsika mtengo kwambiri padakalipano zomwe alimi sadayembekezere kuti zingatero popeza malonda adayamba bwino mmadera ambiri. +Pamene ena akolola nandolo, wina akadali mmunda kuti aume bwino Kapalasa, yemwe ndi gogo wa zilumika zoposa 90, adati chiyembekezo chake pa mbewuyo chayamba kumira mmadzi popeza lingaliro loti apeza makwacha a nkhaninkhani pakutha pamsikawo, ayamba kukayikitsa. +Kuno alimi ambiri tapeza nandolo wochuluka koma tsopano tagwira njakata ndi momwe zilili pamsika popeza miyezi yapitayi nandolo tinkagulitsa pa mtengo wa K600 pa kilogalamu koma tsopano lero wafika pa K300 pa kilo. Kutsika kotereku sikunachitikepo nkale lonse, adatero Kapalasa. +Iye akuganiza kuti mchitidwewu nkubera alimi omwe amadalira ulimi wokhawo pa chaka kuti apeze makwacha otukulira banja lake. +Chaka chino chimanga sichinachite bwino kudera lino moti anthu ambiri tayamba kale kukumana ndi mavuto adzaoneni ndi kukwera kwa mtengo wa chimanga popeza thumba la chimanga cholemera makilogalamu 50 lafika kale pa K12 000. Maso athu adali nganganga pa nandolo kuti mwina tikagulitsa tipeza ndalama zogulira chimanga, koma pamenepa tasowa pogwira, anadandaula iye. +Kapalasa akufunitsitsa boma likadalowererapo msanga ncholinga choti alimi apeze phindu lokwanira pa ulimiwo. +Gogoyo akuganiza kuti kupanga magulu zingathandize alimiwo kupeza phindu lamnanu pa ulimiwo. +Alimi ambiri mboma la Mulanje adakolola nandolo wochuluka ndiponso wina adakali mminda kulindira kuti awume moyenera. +Masiku apitawo mkulu wa bungwe la alimi a nandolo la Nandolo Association of Malawi Susan Chimbayo adapempha alimi kuti asagulitse msanga nandolo wawo, komanso kuti akonze magulu kuti azikagulitsa ku makampani kumene mtengo umakhalako bwino. +Akwiya ndi bungwe la MEC Mpungwepungwe umene ukuchitika kubungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) wakwiyitsa zipani zotsutsa komanso omenyera ufulu omwe apempha kuti zinthu zikonzedwe msanga kubungweli kuti ntchito yochititsa zisankho isaime chifukwa kutero nkuphwanya ufulu wa anthu wosankha atsogoleri awo. +Mneneri wa chipani cha Peoples Party (PP) Ken Msonda, komanso wa chipani cha UDF Ken Ndanga kudzanso mkulu womenyera ufulu wa anthu, Unandi Banda, apempha bungweli kuti likonze zinthu msanga kuti zipani zonse zikhale ndi chikhulupiriro pa bungweli. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Msonda: Sitikukondwa nazo zimezi Ndemanga za akuluakuluwa zikudza pamene kubungweli kwachitika zingapo monga kulephereka kwa zisankho zachibwereza mmadera asanu; kusokonekera kwa ndalama; kutumizidwa kutchuthi kwa akuluakulu ena a bungweli mokakamizidwa; komanso pamene bungweli likutha masiku opanda wapampando chimwalirireni mwadzidzidzi amene adali mtsogoleri Maxon Mbendera. +Msonda adati zomwe zikuchitika ku MEC zikuonetseratu kuti bungweli silikugwira ntchito mokomera zipani zotsutsa. +Kutumiza ogwira ntchito ena kutchuthi ndi nkhani yabwino, chifukwa tikufuna tidziwe momwe ndalama [zoposa K15 miliyoni] zidasowera. Koma vuto lathu ndi kuimitsa zisankho [zapaderazi] kuti zisachitike. +Ife sitikukondwa nazo, zikuonetseratu kuti bungweli likunjenjemera ndi boma. Ichi nchipongwe kuti zisankho zapadera zisachitike. Tadandaula nazo, adatero Msonda. +Iye adati kusachititsa zisankho zapaderazi ndi kuwaphwanyira ufulu anthu a maderawo chifukwa ntchito zachitukuko komanso zakumtima kwawo sizingapherezere kaamba kosowa wokatula nkhawa zawo ku Nyumba ya Malamulo kapena kukhonsolo. +Naye Ndanga adati chikuwadandaulitsa iwo si kuimitsidwa kokha kwa zisankho chachibwereza, koma kuti izi zingakhudze chisankho cha 2019. +Ntchito yochititsa chisankho simangochitika tsiku limodzi, ndi ndondomeko yomwe imachitika kwa nthawi yaitali. Nanga poti anthu ena kulibeko, ntchito igwirika bwanji? Izi tikudandaula nazo, adatero Ndanga. +Mogwirizana ndi akulu a zipani ziwirizi, Banda adati kutumizidwa kutchuthi kwa akuluakulu ena komanso kusowa kwa mtsogoleri wa bungweli ndi nkhani yaikulu komanso yodandaulitsa. +Mwachidule, izi zikutanthauza kuti tilibe bungwe loyendetsa zisankho. Bungweli limakhalapo ngati lili ndi mtsogoleri komanso ena omuthandizira. Ndiye bungwe lilipo? akudabwa Banda. +Koma mkulu wa nthambi yoona za chuma kubungweli, Linda Kunje, akuti anthu asadandaule chifukwa zonse zilongosoka. +Palibe chovuta ndipo zipani zisadandaule, adatero Kunje. +Malamulo a zisankho amati pasadutse miyezi itatu dera lisadachititse chisankho chopeza mtsogoleri chichokereni kapena chimwalirireni mtsogoleri amene adalipo. Kunje aadati akudziwa za izi komabe sangachitire mwina. +Inde taphwanya lamulo koma sitingachitire mwina chifukwa pali zifukwa zomveka zomwe zatilepheretsa kuchititsa zisankhozi, adatero Kunje. +Emmanuel Ngwira: Katswiri wa vimbuza Gule wa vimbuza si wachilendo kwa Amalawi ambiri. Takhala tikuona guleyu akuvinidwa mmawailesi akanema osiyanasiyana. Lachinayi lapitali mtolankhani wathu Martha Chirambo adacheza ndi katswiri wa guleyu Emmanuel Ngwira yemwe amavina vimbuza. Ngwira ndi mtsogoleri wagulu lovina la Kukaya lomwe lidayamba mchaka cha 2005. Kucheza kwawo kudali motere: Ngwira: Ndimadzichepetsa Kodi Emmanuel Mlonga Ngwira ndi ndani? Ndine mzibambo wa zaka 43. Ndili pa panja ndi ana atatu. Mkazi wanga ndi namwino pa chipatala cha Rumphi. Ndimachokera mmudzi mwa Zinyongo Makwakwa, T/A Mpherembe mboma la Mzimba. Timakui ku Elunyeni. Uku nkomwe ndakulira, kuphatikizirapo ku Chikwawa ndi mzinda wa Mzuzu. Moti sukulu yanga ya sekondale ndidaphunzira pa sukulu ya Katoto ndipo kuchoka apo ndakhala ndikuchita maphunziro osiyana osiyana okhudza za maimbidwezi. Ndine mkhirisitu wa mpingo wa Katolika. +Ndili ndi certificate yochokera ku sukulu ya ukachenjede ya Pretoria koma ndinkaphunzilira konkuno ku Centre for Indigenous Instrumental for African Dance Practices. Ndidachita maphunzirowa kwa zaka ziwiri. +Kupatula apo ndilinso ndi certificate mu zoimbaimba yochokera ku Chancellor College. +Mbanja la mai wanga ndidabadwa ndekha pamene powerengera ku banja lina ndingati tilipo anthu asanu. +Udayamba bwanji kuvina vimbuza? Izitu nza mmagazi. Zidachokera ku makolo chifukwa choti mai anga adali a Vimbuza. Iwo sankavina ayi; koma adali ngati asinganga chifukwa ankalota ndipo munthu wolotedwayo amabweradi kudzafuna mankhwala kwa iwowo mpaka kuchira. +Nanga udayamba liti? Ndidayamba kuvinaku mchaka cha 1995 pomwe wansembe wina wampingo wa katolika Reverend Alex B Chima yemwe adali ndi gulu lake la Kukwithu Troop patchalitchi ya St Peters mu Mzuzu Diocese. +Atandiona kuti ndili ndi maluso osiyanasiyana, adanditenga dziko lonse la Malawi kuchita kafukufuku wa zomwe zimachitika kuti munthu azivina. Adatifunsa ngati wina mwa ife ali ndi gule woti gulu lathu lingamavine, ndidayambitsa guleyu ndipo ndidaphunzitsa anthu nyimbo. +Kuchokera nthawi imeneyo ndidayambapo kupititsa patsogolo luso langa. +Kodi muli ndi vimbuza kapena? Ayi ndithu. Ine ndimangovinapo ngati gule basi. Ndilibe vimbuza ndine wabwinobwino ndithu ndilibe mizimu yoipa. Ngakhale mutapita kumalo osungirako zinthu zakale zopatsa chidwi a Mzuzu Museum, mukapeza kuti kuli zithunzi zanga zomwe adajambula nditapambana pampikisano womwe udachitika ku Rumphi. Ndidapikisana ndi asinganga 34. +Kodi nchifukwa chani mumavina guleyu? Pali zifukwa zinayi zomwe ndimavinira guleyu monga: Kusangalatsa anthu, kuwaphunzitsa zosiyanasiyana kudzera mmagule, kusunga chikhalidwe komanso kupititsa patsogolo chikhalidwe. +Kodi anthu amati chani za inu. +Kuchokera kubanja langa, ndakhala ndikunenedwa kuti bwanji ndimavina magule osiyanasiyana. Anthu amandiyankhula zambiri zosiyanasiyana ndipo amanditenga ngati sindimadziwa zomwe ndikuchita koma ineyo ndimakhulupilira kwambiri mizimu. Mayi ndi bambo anga adamwalira kalekale komabe ndimakhulupilira kuti mizimu yawo imanditeteza. Ichi ndi china mwachifukwa chomwe ndimavina modzipereka kwambiri ndipo anthu amandipatsa ndalama zambiri. +Mumavinanso magule anji? Mwa ena ndimavina mganda, malipenga ndi chilimika zochokera ku Nkhata Bay, mapenenga a ku Karonga, beni kuchokera ku Mangochi komanso mwinoghe a ku Chitipa. +Chenjerani, 2017 tisatuwe ndi njala Lero ndi tsiku lakutha kwa chaka cha 2016. Pomwe masiku athera kuchitseko ndipo chaka cha 2017 chili pamphuno, akadaulo ena a zaulimi ati alimi asagone mchaka chikudzachi kuti mwina mavuto a njala amene akhala akupana Amalawi zaka ziwiri zapitazi asatisautsenso. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Yemwe anali mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a zaulimi la Civil Society Agriculture Network (CisaNet), Tamani Nkhono-Mvula adati mphamvu zili mmanja mwa alimi kuti chaka chikudzachi kusakhale njala. +Mu 2015, mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika adalengeza kuti dziko lino lili pangozi kaamba ka madzi osefukira amene adasautsa mchakacho. Koma paulimi wa 2015-2016, mvula idadula msanga zimene zidachititsa kuti zokolola zitsike. +Anthu kumalo ogulira feteleza a Optichem mwezi watha Njala yakhudza Amalawi 6.8 miliyoni chaka chino moti mabungwe, boma ndi ena akhala ali pakalikiliki kuthandiza Amalawi ndi chakudya. +Pomwe mvula chaka chino yadza ndi mkokomo, mantha ali chaka chikudzachi kuti mwina anthu aonanso mdima ndi njala yomwe ingagwe. +Koma Nkhono-Mvula akuti mantha angathedi kuchuluka ngati alimi angaseweretse mvula yomwe ikugwayi. +Tidauzidwa kale kuti chaka chino kuli La Nina ndipo mwaona nokha momwe mvula ikugwera mmadera onse a dziko lino. Sitikuyenera kuyiseweretsa. Aliyense abzale nthawi yabwino kuti ikamasiya, mbewu zikhale zili pena, adatero Nkhono-Mvula. +Iye adati ndi bwinonso alimi abzale mbewu zosiyanasiyana kuti chimanga chikavuta adzaone populumukira. +Ngati tili ndi La Nina, ndiye kuti tilandira mvula yambiri, mvula imeneyi tisangoyirekerera, tiyeni tibzale mbewu zina monga mpunga, chinangwa, mbatata ndi zina kuti madziwa atithandize, adatero Nkhono-Mvula. Mkulu wa bungwe la Farmers Union of Malawi (FUM) Alfred Kapichira Banda wati chaka chikudzachi pali chiopsezo cha njala chifukwa boma silinaikepo mtima pantchito yogawa makuponi ogulira feteleza ndi mbewu zotsika mtengo. +Tikunena pano, madera ena sanalandirebe makuponi. Ichi ndi chiyambi cha njala. Alimi ambiri abzala, chimanga chawo chakula kwambiri moti chikufunika feteleza koma nzachisoni kuti feteleza wa makuponi sadafike. +Achikhala boma lidachfulumira ndi ndondomeko ya feteleza, si bwezi tikudandaula ndipo bwezi tikunena molimbika kuti chaka chikubwerachi sitikhala ndi njala monga zidalili zaka zapitazi, adatero Banda. +Mchaka chikuthachi, kudagwa dzombe limene lidachecheta mbewu zambiri komanso lidaika pachiopsezo Amalawi amene ankadya dzombe lophedwa ndi mankhwala amene adapoperedwa. +Nayo misika ya Admarc idatsegulidwa mochedwa mchakachi ndipo chimanga chimnagulitsa mokwera kuposa kwa mavenda. Thumba lolemera ndi makilogalamu 50 limagulitsidwa pa mtengo wa K12 500. Izi sizidakomere Amalawi ndipo mapeto ake samapita kukagula chimangachi. +Sitalaka pa Wenela Lidali Lachinayi usiku ndipo tidali malo aja timakonda pa Wenela kukambirana izi ndi izo. Adachuluka adali madilaivala ndi makondakitala a minibasi. +Ife ojiya, osenza ndi osolola tidalipo ochepa. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Apapa afune asafune, mawa kulibe woyendetsa minibasi kuchoka pano pa Wenela, adayamba nkhani mmodzi mwa madalaivala. +Komatu tikanaganiza kale. Mawalo msuzi tikaupeza kuti? adafunsa kondakitala wina. +Koma akanadziwa! Anzakewo adamuukira, kumuthira maphuzo, monga achitira anthuwa pamsewu! Nkhani yavuta ndi ya msuziyo! Mabwana aja akamangala papolisipa kuti akatigwira tizilipira ndife osati mabwanawo. Msuzi uzikwaniranso apapa? adafunsa wina bata litabwerera. +Koma inuyo chikuvuta nchiyani makamaka kuti zifike apa? adafunsa Abiti Patuma. +Kodi ndiwe mlendo? Apolisi ayamba kugwiritsa ntchito malamulo amene akutipweteka kwambiri. Sitikufuna zimenezo, adatero wina. +Kodi malamulowo ali mmabuku? adafunsanso Abiti Patuma. +Kodi ukufuna kuvuta bwanji? Kapena ndi zibwenzi zako? Malamulowo ndi wokhazikika kungoti samawagwiritsa ntchito ndiye pano akufuna kutifinya, adayankha mkulu wina, mmaso muli gwaaa! Komatu tinzeru tikucheperako apapa. Ndikuona kuti mutichedwetsa nazo. Tsono mukayamba kuchita zionetsero zokwiya ndi malamulo okhazikika, simukuona kuti masiku akubwerawa nawo ogwiririra adzachita zionetsero kuti chilango cha zaka 14 kwa opezeka olakwa chakula kwambiri? adaponya funso lina Abiti Patuma. +Onse adangoti duuu! Ngati malamulo mukuona kuti akhwima kwambiri, mukadakambirana ndi aphungu anu kuti akasinthitse izi ku Nyumba ya Malamulo. Wina akhoza kubwerapo ndi Minibus Regulations Bill. Osati zanu za umbuli mukuchita apazi, adapitiriza. +Palibe, kaya wina afune kaya asafune, ife tikukachita zionetsero basi, adatero wina, akutulutsa chikwanje. +Adachinola pamsewu. +Mawa lake ndiye kudali moto. Ndidaona anthu akuyenda wapansi kuchoka ku Ndirande mpaka mtauni. Ochokera ku Machinjiri adali kukwera malole. Ku Manja ndi Chimwankhunda ndiye tidamva za kuphwanyidwa kwa galimoto zina. Eyi! Eyi Eyiiiiii! Posafuna kutsalira, zigandanga za ku Machinjiri zidaotcha khoti chaka chatha zidathira moto maofesi apolisi atatu. Ati kusafuna kumangidwa. +Pomwe moto umazilala Loweruka, madalaivala aja adagwirizana zokweza mtengo wa minibasi. +Abiti Patuma adati ndimuperekeze ku Queens. Pa Mibawa, adati mtengo wakwera kuchokera pa K200 kufika pa K250. +Chifukwa? adafunsa. +Kaya, adayankha kondakitala. +Abiti Patuma adalipira K500 ya anthu awiri. Kenaka adatangwanika pa WhatsApp. Sindikudziwa ankalemba chiyani, koma uthenga womaliza udali woti: Tikumana pachipatala pasiteji. +Titafika pasitejipo, tidapeza kuti amalankhula ndi anzake awiri. +Kwerani ndalipira kale kuchoka mu Blantyre ya anthu awiri. Asakulipiritseninso ameneyu. Akachita makani, manambala aapolisi aja si nkhani. Anthu ogenda kupolisi chamba chili mthumba awa, adatero Abiti Patuma. +Lonjezo la jb Lasanduka loto Bambo ake adamwalira, chiyembekezo chidali pa bambo womupeza, nawonso adamukhumudwitsa pomugwiririra nkumupatsa pathupi ndipo bwalo la milandu lidamugamula kuti akaseweze kundende zaka 13. Moyo wakhala wowawitsa; loto lodzakhala wapolisi lidasanduka la chumba. +Escom in free-for-all fuel scam Wait gets longer Secrecy over party funders Koma pa 18 March 2013, chiyembekezo cha Zione (tangomupatsa dzinali) chidatukusira pamene yemwe adali mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda adamulonjeza kudzamulipirira maphunziro ake mpaka kuyunivesite. +Malinga ndi mphunzitsi wa Zione, Dziwa Nazombe-Mbewe, Banda adalonjeza Zione patsiku lomwe amayendera ku One-Stop-Centre kuchipatala cha Queen Elizabeth Central mumzinda wa Blantyre. +Patsikulo ogwira ntchito ku One Stop Centre adandiimbira kuti apulezidenti akhala akuyendera malowo ndiye akufuna Zione akalankhule zomwe zidamuchitikira. +Ndidapita naye ndipo apulezidenti adafika mchipinda chathu momwe adacheza ndi Zione yemwe panthawiyo adali ndi zaka 13. Atamufunsa za sukulu, iye adati akufuna apitirize. Apa mpamene apulezidenti adati amulipirira sukulu yake, adatero Nazombe-Mbewe. +Tsogolo sakuliona: Zione (kumanzere) ndi aphunzitsi ake Mayi Nazombe-Mbewe Iye adati Banda adauza mayi Lingalireni Mihowa amene adali nawo panthawiyo kuti ndiwo azilumikizana nawo pankhani ya thandizolo. +Chimwemwe chidadza ngati mmawa kwa Zione, zoti adachitidwa chipongwe ndi bambo ake, zidaiwalika. Tsopano loto lodzakhala wapolisi lidayamba kuoneka tsogolo lake. +Ndidali ndi chimwemwe. Titangotuluka, ndidaimbira foni malume anga ku Balaka komanso kudziwitsa anzanga akusukulu zomwe apulezidenti adandilonjeza, ndidasangalala kwambiri, adatero Zione. +Chidatsala nkuti Zione, yemwe panthawiyo adali Sitandede 8, akhoze mayeso. Ndidakalimbikira kusukulu ndipo ndidakhozadi, adatero. +Apa mpamene mphunzitsiyu adakambirana ndi Mihowa kuti Zione akalowe Fomu 1 kusekondale. +Ndidapita kuofesi kwawo ndipo tidakambirana poti panthawiyo nkuti Zione adali asadabereke, adati tidikire abereke kaye kuti abwerere kusukulu, adatero Nazombe-Mbewe. +Pa 9 January 2014, mwana adabadwa ndipo ati adagwirizana kuti pakatha miyezi 7 Zione akayambe sukulu. Mu July mwana adamuleketsa kuyamwa kuti abwerere kusukulu. +Nazombe-Mbewe adayesera kutsatizira nkhaniyo koma sinaoneke mutu wake. +Ndidapita kuofesi kwawo ndipo adati andiimbira. Poona kuti sakuimba, ndidapitanso ndipo adandiuza kuti ndisiye nambala aimba, koma sadaimbe. Ndidadzapitanso pamene adati ndilembe nkhani ya Zione ndipo aitsatizira koma sizidatero mpaka lero pamene ndatopa, adatero Nazombe-Mbewe. +Ngakhale mphunzitsiyu adalembera ofesi ya Mihowa kalata zokumbutsa za lonjezolo, komabe palibe chidachitika mpaka lero. +Msangulutso utaimbira foni Mihowa, iye adati tilankhule ndi Levi Mwase amene amayendetsa nkhaniyo. Koma Mwase adati sindine mneneri wa Joyce Banda, imbirani mneneri wake Tusekere Mwanyongo. +Mwanyongo adati nzovuta kuti anene chifukwa chenicheni chomwe lonjezolo silidatheke koma wati mwina padalibe kulumikizana kwabwino. +Mayi Joyce Banda akhala akuthandiza ndipo mpaka lero akuthandizabe ana ambiri asukulu. Nkutheka kuti padalibe kulumikizana kwabwino ndi mtsikanayo, adatero. +Koma mthandizi wa Banda, Andekuche Chanthunya, akuti ndondomeko zoyenera sizidatsatidwe nchifukwa mtsikanayu sadathandizidwe. +Samayenera apite kwa Mihowa koma abwere kwa ine kapena kwa Levi [Mwase]. Ngati akufuna kuthandizidwa akuyenera atsatire ndondomeko, adatero. +Njovu zikamamenyana udzu ndiwo umavutika. Kuponyerana Chichewaku sikukuthandizabe Zione amene pano akusungidwa ndi banja lina ku Chirimba mumzinda wa Blantyre. +Banja lomwe likusunga Zione silingakwanitsenso kumutumiza kusukulu. Bambo wa pabanjapo, Evance Milanzie wati moyo wa Zione wafika pomvetsa chisoni. +Ndi mwana wanzeru, zangovuta kuti lonjezolo silidatheke, adatero Milanzie. +Aka si koyamba kuti mtsogoleri wa dziko alonjeze mwana koma osakwanitsa lonjezolo. Mu 2004, mtsogoleri wakale Bingu wa Mutharika adalonjezanso Marietta Mhango wa mmudzi mwa Mawelera kwa Paramount Kyungu mboma la Karonga kuti adzamulipirira sukulu. +Mutharika adalonjeza Marietta pamsonkhano kuti adzamulipirira atanena bwino ndakatulo, koma ngakhale adatsindika za thandizolo, izi sizidatheke ndipo lero Marietta akutuwa. +Kodi izi zimatero chifukwa chiyani? Mphunzitsi wa zandale kusukulu ya Chancellor Collage Joseph Chunga akuti mtima wofuna awaone ndi omwe umachititsa. +Amafuna kuti mwina aoneke kuti ali ndi mtima wabwino, cholinga akalonjeza apateko mavoti chifukwa cha mtima womwe aonetsa, koma nzachisoni, adatero Chunga. +Pamene izi zili chonchi, Zione ndi wokhumudwa ndipo zasokoneza moyo wake. Katswiri kumbali ya kaganizidwe ka munthu, Chiwoza Bandawe akuti Zione kukhala wachichepere, izi zingakhudze moyo wake. +Atsatsidwa kugula anthu kawiri Njonda ina yomwe ikuchita bizinesi yake ya golosale ndi chigayo pa boma ku Dowa yadandaula kuti anthu akuiwonongera mbiri chifukwa yatsatsidwapo anthu kawiri konse. +Stanley Ishmael adauza Msangulutso kuti zimenezi ndizongofuna kumuonongera mbiri yake chifukwa iyeyu sagula anthu. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Anthu akakhala, basi amangoganiza kuti timapanga zimenezo, koma sichoncho. Sindipanga zimenezo, adatero Ishmael. +Malinga ndi Ishmael, miyezi yapitayo, amayi ena adafika pagolosale yakeyo kukatsatsa amuna awo pomwe sabata yatha mnyamata wina adamutsatsa msuweni wake wa zaka 20 pomutchula kuti nkhuku yoyera. +Ishmael adalongosola kuti adadzidzimuka sabata yathayi ataitanidwa ndi mzake wina kuti kwabwera kalata yake kuchokera kwa mkulu wina wa zaka 26 wochokera mmudzi mwa Chinyanya T/A Chiwere mboma la Dowa. +Mkalatamo adalongosola zoti wakhala akulota katatu konse ndikumufunsa ngati ali ndi nkhuku yoyera, adalongosola Ishmael. +Iye adati apa awiriwo adamuitanitsa mkuluyo kuti adzawalongosolele zomwe amatanthauza mkalatamo. +Apa adatiuza kuti umphawi wamuvuta ndipo ali ndi munthu woti akufuna kundigulitsa. Izi zidandiopsa ndipo ndidakaitula nkhaniyi kupolisi komwe adandiuza zochita, adatero Ishmael. +Iye adati mkuluyo adamtumiza msuweni wake wa zaka 20 yemwe amamtsatsayo kugolosale ya Ishmael ati kuti akamuone. +Malinga ndi Ishmael, adamuitanitsanso mkuluyo kuti adzalongosole bwino za malondawo. +Sadachedwe ayi. Adabweradi, apa nkuti nditawauza kale apolisi ndipo apolisiwo adatipeza tikukambirana za mtengo womwe panthawi yomwe amammangayi adali asadatchule, iyer adatero. +Koma Ishmael adati apolisiwo atangofika pamalopo mkuluyo adayamba kukana kuti sichoncho, koma apolisi adamumanga kuti akayankhire komweko. +Pewani ngozi, kuberedwa Nyengo ya Khirisimasi ndi Nyuwere kumachuluka ngozi za pamsewu, mchitidwe wa umbava ndi umbanda komanso ngozi zina monga kumira mmadzi akusangalala. +Nthambi yoona za ngozi za pamsewu ya Directorate of Road Traffic and Safety Services (DRTSS) yakhala ikupereka malangizo kudzera mnyuzipepala kuyambira pa December 14 2016 pofuna kuti anthu adziwe msanga za kapewedwe ka ngozi zisangalalo zisadafike pachimake. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ngozi iyi idachitika sabata yangothayi Nthambiyi yati kupatula zopangitsa ngozi zina, nkhani yaikulu imakhala kuyendetsa galimoto chiledzerere kapena galimoto zosayenera kuyenda pamsewu zomwe zimaononga miyoyo ndi katundu. +Chikalatacho chidatinso oyendetsa galimoto akuyenera kupereka mpata odutsa kwa anthu mmalo monse mowolokera ndipo asayankhule palamya akuyendetsa galimoto poopa kuti chidwi chawo chingathawire ku lamyako mmalo moyendetsa galimoto. +Nthambiyo idatinso okwera ali ndi udindo odziteteza popewa kukwera galimoto zomwe zadzadza kwambiri ndi kupewa kukakamiza oyendetsa kuti azithamanga ngati achedwa paulendo wawo. +Nawo apolisi ati anthu ali ndi udindo woteteza miyoyo ndi katundu wawo potsatira ndondomeko zomwe iwo amapereka chaka ndi chaka monga kuonetsetsa kuti asiya munthu okhwima maganizo pakhomo akamachoka. +Mneneri wa polisi James Kadadzera adati nthawi zambiri chifukwa chokomedwa, anthu amasiya pakhomo palibe aliyense nkupita kokasangalala ndipo pobwera amapeza nyumba yathyoledwa. +Njira ina nkuonetsetsa kuti pomwe ana akusewera kapena kusangalala, pali munthu wamkulu owayanganira kuopa kuti angabedwe kapena kuvulala ngati ali okhaokha, adatero Kadadzera. +Mkangano wa mafumu sukuzirala Ntchito za chitukuko zagwedera mboma la Neno, Nsanje komanso Salima kaamba ka mpungwepungwe wa mafumu womwe sukutha. +Ku Neno boma lidathotha mfumu Chekucheku mu 2014. Mpaka lero boma silidabwezeretse mfumuyi zomwe zapangitsa kuti ofesi ya DC ndi khansala asowe wogwira naye ntchito za chitukuko. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Chekucheku amene akudikira boma limubwezeretse DC wa boma la Neno, khalansala komanso phungu wa Nyumba ya Malamulo kumeneko akuti mdera la Chekucheku chitukuko chikuvuta chifukwa palibe mfumu yeniyeni yomwe angagwire nayo ntchito. +Nako ku Nsanje, boma lidaimitsa mfumu Chimombo ndipo lidapatsa mphamvu Harrison Chimombo kuti abagwirizira. Mpaka lero boma silidapezebe wolowa mmalo mwake zomwe zapangitsa kuti anthu agawanike. +Mfumu Bibi Kuluunda ya ku Salima yomwe idaimitsidwa paudindo ndi boma akuti maso ake ali ku boma kuti amubwezeretse ufumu wake chifukwa iye ndiye woyenera ufumuwo. +Boma lidaika mbale wa mfumuyi kuti agwirizire ufumuwu kufikira mpungwepungwe utazirala. +Mafumuwa ndiwo amathandizira kuti chitukuko cha paboma lawo chiyende bwino pogwira ntchito ndi makhansala, ofesi ya chitukuko pa boma, komanso ofesi ya DC. +Koma mneneri wa ku unduna wa za maboma angono Muhlabase Mughogho akuti bata lidzabwerera pokhapokha eni banja atadya khonde ndi kutulutsa munthu woyenerera amene angagwire ntchito ndi boma. +Tili ndi gawo lothandizira komabe mphamvu zili mmanja mwa abanja kuti atipatse mfumu, adatero Mughogho. +Mughogho akuti boma silivomereza mfumu yogwirizira. Dziwani kuti boma siligwira ntchito ndi mfumu yogwirizira. +Izi zikutanthauza kuti ku Salima, Nsanje ndi Neno kulibe mafumu omwe boma lingagwire nawo ntchito. +Naye DC wa ku Neno Ali Phiri adapempha abanja kuti atulutse munthu amene angalowe mmalo mwa mfumu Chekucheku amene adachotsedwa, koma mwadzidzidzi kudaperekedwa maina asanu. +Sizikadatheka kuti onse angakhale mfumu nthawi imodzi. Zidakanika. Ndiye ndivomereze kuti mpaka pano tilibe mfumu Chekucheku, adatero Phiri. +Phiri adati akugwira ntchito ndi makomiti azachitukuko akumudzi chifukwa chosowa mfumu zomwe adati nzovuta. Komabe chitukuko chikutheka ngakhale zina zikufunika amfumu. +Khansala wa dera la Chikonde kwa mfumu Chekucheku, MacPherson Dzimadzi adati ntchito yomanga midadada pa sukulu ya Kalioni ndi Chiwamba ikukanika chifukwa chosowa kwa mfumu Chekucheku. +Pali ntchito yotuta mchenga, njerwa komanso kwale yomwe ikukanika. Ndidauza mafumu angonoangono kuti atsogolere anthu awo koma zikukanika chifukwa palibe wamkulu amene angawalankhule. Nthawi zina ndikumaweruza milandu ya mafumuwa akayambana nthawi zina ndikumawatengera kwa DC, adatero Dzimadzi. +Ndivomere mavuto alipo chifukwa chosowekera kwa mfumu Chekucheku, adaomba mkota Dzimadzi. +Malinga ndi ndime 23:03 gawo II gawo la malamulo okhudza mafumu, boma lidaimitsa mfumu Chekucheku yemwe dzina lake ndi Francis Magombo kuti asagwirenso ntchito za ufumuwu mboma la Neno kuyambira pa 15 May 2014. +Lachiwiri msabatayi, Chekucheku adauza Tamvani kuti akudikirabe boma limuvomere kuti ayambirenso kugwira ntchito. +Ufumu umene uja ndi wanga ndipo ndikungodikira mtsogoleri wa dziko lino kuti andibwezeretse pa mpandopo, adatero. +Ku Nsanje mamembala ena abanja la mfumu Chimombo adalembera DC wa bomalo, komanso unduna wa maboma angono kuti asabwezeretse Chimombo amene adachotsedwa mu December 2012. +Mfumu yochotsedwayo, Stanford Tukula, idachotsedwa pamene imaganiziridwa milandu yosowetsa katundu. +Ku Salima boma lidaimitsa mfumu Kuluunda, Khadija Habib Saidi, mu May chaka chatha chifukwa chomuganizira ziphuphu. +Mpaka lero boma silinabwezeretse mfumuyi ndipo mbale wake wa mfumuyi ndiye akugwirizira ufumuwo. +Pocheza ndi Tamvani Lachiwiri, mfumuyi idati ndikudikirira aboma kuti andibwezeretse pampando. +Koma katswiri pa zandale Henry Chingaipe mmbuyomu adauza Tamvani kuti dziko lino silidafike pomagwira ntchito yake popanda mafumu. +Pakufunika Chiefs Act [Malamulo okhudza mafumu] atakonzedwanso kuti tidziwe ntchito za mafumu komanso za mtsogoleri wa dziko pa nkhani zokhudza mafumu, adatero. +Sitidafikepo pomagwira ntchito popanda mafumuwa, ndiwofunikabe koma pokhapokha titadziwa ntchito zawo pamene tili [mu ulamuliro wa zipani zambiri]. +Mkulu woyendetsa nkhani zachitukuko ku Neno, Henry Chitema, akuti kusowekera kwa mfumu Chekucheku kwasokoneza nkhani zachitukuko. +Chitema akuti mfumuyi imayenera kutsogolera anthu ake ndi mafumu ake kuti agwire ntchito za chitukuko. +Ena tikawauza kuti tigwire ntchito akumatiuza kuti iwo ndi abanja lachifumu kotero sangagwire ntchito, adatero. +Boma la Neno lili ndi mafumu anayi panopa tatsala ndi ma T/A atatu. Tilibe amene angayimire anthu a kwa Chekucheku. Izi zatikhudza. +Wapitadi Gwanda Ngati bodza Lachisanu lapitali walowadi mmanda Gwanda Chakuamba, mmodzi mwa amkhalakale pandale mdziko muno. +Mmene chitanda cha malemu Chakuambayemwe mmaboma a Nsanje ndi Chikwawa kuchigwa cha Shire ankamutcha Mbuya pomulemekeza chifukwa cha zabwino zambiri zomwe adakhala akuchitira anthu a kuchigwachi ali moyo, chimatsikira mmanda ku Chinyanje kwa T/A Mlolo, kuseri kwa nyumba yake yotchedwa Zuwele Castleambiri sadathe kuigwira misozi. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Maliro a Chakuamba adalandira ulemu wapadera poikidwa ndi asirikali a nkhondo a MDF Ndi mitima yosweka ambiri adalira: Wapita Mbuya, wapita Mbuya! Amayi a Dorica a Muona Seventh Day Adventist adaimba mobwerezabwereza: A Chakuamba ku Nsanje, a Chakuamba ku Chikwawa kutanthauza kuti Chakuamba adali mwana wa maboma awiriwa. +Mizwanya ina yodziwika pandale yomwe idabwera kudzaperekeza Mwana Mphenzi ndi mtsogoleri wakale Bakili Muluzi, Sipika wakale Chimunthu Banda, Brown Mpinganjira, Sidik Mia, Kamlepo Kalua, Nicholas Dausi, Harry Thomson, Bazuka Mhango, akuluakulu a zipani za MCP, UDF ndi DPP ndi akuluakulu a boma motsogozedwa ndi mlembi wamkulu mu ofesi ya Pulezidenti ndi Kabineti George Mkondiwa, kungotchurapo ena pangono. +Inde kudali chinamtindi cha anthuolira ndi ongoyangana, amipingo yosiyanasiyana ndi osapemphera omwe, koma onse okhala ndi cholinga chimodzi: kudzaperekeza munthu yemwe mbiri yake sidzaiwalika mmbiri ya dziko la Malawi ngati mmodzi mwa anthu amene adamenyera ufulu wa dziko lino kuchoka mmanja mwa atsamunda kufikira lero lino pamene dzikoli lili paufulu wodzilamulira. +T/A Malemia amene adalankhula mmalo mwa T/A Mlolo pamaliropo, adati ngakhale akulira, koma ndi osangalala kuti kudera la chigwa cha Shire kudachoka munthu wodzipereka ndi wokonda anthu ake ngati Chakuamba yemwe dziko la Malawi silidzamuiwala. +Sitidzapezanso Chakuamba wina kuno. Uyu ndiye adali weniweni; wangwiro, wachilungamo, wosaopa, mkhalakale pandale. Watiphunzitsa kukhululukirana ndi kugwirana manja ngati tifuna kuti dziko lathu litukuke. Uku kudali kulira kwa Paramount Lundu. +Ena adayerekeza Chakuamba ndi malemu Nelson Mandela mtsogoleri wakale wa dziko la South Africa, pokhululukira chipani cha MCP, chomwe chidamangitsa nkumuponya mndende kwa zaka 14, koma atatuluka kundendeko adalowanso chipani chomwecho nkumagwira ntchito limodzi ndi omwe adamum-angitsawo. +Pa ichi, Malemia adati Chakuamba adali munthu wosasunga mangawa ndipo ankalankhula akaona kuti zinthu zikulakwika, zomwe zinkamuika mmavuto nthawi zambiri. +Chakuamba adali wokonda sukulu ndipo kuno waphunzitsa anthu ambiri, Malemia adatero. +Ndipo ena mwa mafumu omwe Msangulutso udacheza nawo adati dziko lino lataya mkhalakale pandale yemwe adatengapo gawo lalikulu pothandizira kulitukula komanso yemwe adali wovuta kumumvetsa pakachitidwe kake mundale. +Inkosi Chindi ya mboma la Mzimba idati idadzidzimuka itamva za imfa ya Chakuamba pawailesi Lolemba lapitali kaamba koti simadziwa zoti wakhala akudwala kwa kanthawi. +Chindi adagwirizana ndi mafumu anzake kuti Chakuamba adali wachitukuko. +Adali munthu wabwino ngakhale munthawi ya ulamuliro wa MCP adali watinkhanza pangono. Paja adadzamenya mafumu kuno kumpoto pamsonkhano waukulu wa chipani mu 1973 ku Marymount mumzinda wa Mzuzu, adatero Chindi. +Iye adati mmodzi mwa mafumu omwe adapatsidwa makofi adali bambo ake chifukwa adakana kupereka ngombe ngati mphatso kwa Kamuzu. +Ndipo mfumu yaikulu Mkukula ya mboma la Lilongwe idati sidzamuiwala Chakuamba chifukwa cha momwe adagwirira ntchito panthawi yothetsa bungwe la MYP. +Mkukula adati Chakuamba ngati mmodzi mwa akuluakulu a boma, adalolera kukambirana ndi kulithetsa bungweli bwino lomwe popanda zipolowe zambiri. +Mmodzi mwa otsata za ndale mdziko muno, Humphrey Mvula, adati Chakuamba adamenyera ufulu wa dziko lino kuchokera nthawi ya atsamunda mpaka nthawi yomwe dziko lino lidathana ndi ulamuliro wa chipani chimodzi. +Malinga ndi Mvula, Chakuamba adali wolimba mtima ndipo sadali wosankha mitundu ngati momwe achitira andale ena omwe amakokera kwawo. +Mvula adati ngakhale Chakuamba sadapambaneko chisankho a mtsogoleri wa dziko lino, adatsala pangono kupambana mchaka cha 2004 pomwe adaimira Mgwirizano Coalition. +Chakuamba adatsikira kuli chete Lolemba lapitali pachipatala cha Blantyre Adventist (BAH) mu mzinda wa Blantyre, naikudwa mmanda ndi ulemu wa asirikali ankhondo. +Amalawi a nsomba ali kakasi ku Botswana Ali mbuu, kutuwa ndi njala, Patricia Mboma ndi wokwiya ndi ganizo la boma la Botswana loletsa kuti mdzikomo musatuluke nsomba kukagulitsa maiko ena. +Si ali yekha, pali ena a dziko la Zambia komanso Botswana. Onse alipo anthu 60 amene agula nsomba zodzadza mathilaki asanu kupita ku Zambia kukagulitsa. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Zina mwa nsombazo ndi zimenezi Mboma, wochokera ku Blantyre, adayamba bizinesiyi mu 2014 kukagula nsomba kunyanja ya Ngami moyandikana ndi Maun kumpoto kwa dziko la Botswana. +Koma ulendo uno wakhala wowawitsa kwa abizinesiwa pamene boma laletsa kutulutsa nsomba mdzikomo ponena kuti silikupindula pa malondawo. +Kuderali anthu ambiri adapeza mgodi wopha ndalama popikula nsomba zouma ndi kukazigulitsa mdziko la DRC kapena ku Kasumbalesa ku Zambia. +Izi zidachititsa kuti mwezi wa March chaka chino, nduna ya zachilengedwe ndi nyama zakunkhalango Tshekedi Khama, mngono wake wa pulezidenti wa dziko la Botswana Ian Khama aletse malondawa. +Pamene amaletsa malondawa, nkuti Mboma komanso anzake atagula kale nsombazo ndipo sadaloledwe kuti apite kukagulitsa. +Kuyambira March mpaka lero, anthuwa akhala akubindikira ku wadi ya Boseje ku Maun. Sabata yatha adathamangitsidwa pamalopo ndipo akubisala ku Kasani kumalire a Botswana ndi Zambia komwe akukanizidwa kudutsa. +Tikupempha boma litilole tipite kukagulitsa nsombazi, adatero Mboma. Ndaononga P30 000 [K2.2 miliyoni] kuti ndigule nsombazi, adatero iye. +Nsomba zambiri zayamba kuola, ntchentche zangoumbirira mathirakiwa. Komabe sindichitira mwina achimwene, ndikuyenera kupita ndi nsombazi ndikagulitse, ndidachita kukongola ndalama yogulira nsombazi. Yochepa yomwe ndingapezeyo ndi yomweyo, adatero Mboma. +Lero vuto lina labadwa pamene eni galimoto akufuna kuti azipita, malinga ndi mabwana awo. Kelvin Kambule amene akuchokera ku Livingstone mdziko la Zambia akuti bwana wake wapindira mlomo wapansi. +Akuimba tsiku lililonse, akuti ndichotse nsombazi ndipo ndizipita. Takhala pano miyezi inayi osapanga chilichonse nchifukwa chake akwiya, adatero. +Thilaki iliyonse yanyamula nsomba za P500 000 [K37 miliyoni] ndipo anthuwa akuyenera kulipira P12 000 [K900 000] kuthiraki iliyonse ponyamula nsombazi. +Komabe boma la Botswana laponda mwala kuti silisunthika pa ganizo lake. Sitilola kuti geniyi ipitirire, mchitidwewu wapangitsa kuti pa nyanja pachuluke asodzi opanda zikalata zowalola kuti aphe nsomba, adatero Khama. +Izi zipangitsa kuti misozi ya Mboma isaleke kukha: Tsiku lililonse tikumasonkherana P5 [K370] kuti tidye. Masiku akatha okhalira mdziko muno tikumapita mmaiko athu kukaonjezeretsa masiku. Adakatimvera chisoni. +Basi ayisempha Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Tsiku limenelo sitidakhale pa Wenela. Palibe ojiya, osolola, osenza ndi oitanira amene adatsala pa Wenela. +Tidakwera galimoto la mkulu wina kulowera ku Lilongwe. Si kuti timapita kuja kulikulu la boma kumene masamu ogula mmera asokonekera. +Sindingakambe nkhani imeneyo chifukwa tonse tikudziwa kuti lingaliro la Dizilo Petulo Palibe, malinga ndi kufotokoza kwa Joloji Chiponda, lidali logula chimangacho ku Brazil. Zoona mpaka kuoda chimanga ku Brazil! Nkhani ya chimangayi kwa ine ndiyongotaya nthawi. Ngati Moya Pete adalamula asilikali ake kukwidzinga uja wogona ndi amayi oposa 100 bwanji akulephera kulamulanso amene akuganiziridwa kukazinga mmera wa tonse pano pa Wenela? Zosamveka konse kuti mzimayi woti akufuna kugula chimanga choti adye pakhomo pake, mmalo mopita yekha kumsikako kutuma wina kuti akamugulire kenako nkumadandaula kuti waberedwa! Abale anzanga, tingoyerekeza kuti mwalemba wantchito, ndiye mukumukaikira kuti anaba ndiwo. Kenako mukuuza akazi kapena amuna anu kuti afufuze momwe anabera ndiwozo, wantchito wanu akapita pachulu nkumakuwa kuti: Sindinabe ine! Sindinabe! Chomwe ndimadabwa pano pa Wenela nchakuti nchifukwa chiyani aliyense amafuna kutalika zala pankhani za chimanga? Tidamvapo kuti Adona Hilida adagulitsa matani ochuluka kupita nawo ku Kenya. Nanga za Thursday Jumbo uja naye adadyapo zake za chimanga. Za makuponi ndiye ndisachite kunena. +Nsataye nazo nthawi izo. +Chaka chino talowa Talowa ndi adani omwe Akufuna moyo wanga Kuti aononge Chauta thandizeni Iyi ndi nyimbo imene tinkamvera mugalimoto ya mkulu amene adatitenga. Tidafika kubwalo la mpira latsopano kumene zipolopolo ndi nyerere zimamenyana. Inu, munthu nkupha nyerere poyiwombera! Ndidangomva kuti ena adathyola mipando, kutenga makalilole ndi zina zotero! Komanso abambo ena ankalowa kuzimbudzi za akazi! Utatha mpira, sindikudziwa kuti udatha bwanji, Abiti Patuma adandikoka kuti timuthawe mkulu uja. +Tidakakwera basi imene sindikuyidziwa bwino. Mudali anyamata a Chimwemwe kwambiri. Iwo amangoti 5 kwa 1, 5 kwa 1. Onse atamuona Abiti Patuma adakuwira limodzi: Abiti Patuma! Yo-yo-yo! Wina adamukumbatira, wina kumupsopsona patsaya. +Osadanda, mwayiphula basi! Ndikuthangatani nonse mbasi momwe muno, adatero Abiti Patuma. +Koma abale! Kudalitu kulandirana! Basi imamveka ndithu kuti mashoko siali bwino komabe mmodzimmodzi adali kulandira chithandizo kuchokera kwa Abiti Patuma. +Adati tinyamuke, ulendo wobwerera pa Wenela. +Tili mnjira, yemwe amaoneka kuti ndi mkulu wa anyamatawo adati: Tikakafika ku Mwanza, tikadzera kwa Ayaya tikayamike chifukwa watithandiza kupeza basi. +Ulendo wa kwa Ayaya sunatheke chifukwa basi idatchona pa Manjawira. Poyamba tinkadya kanyenya kuti mwina iyenda. Kenako kudali kusaka mango, ngumbi ndi zina mpaka mdima udagwa. +Chilengedwe chibwerere ku Mwanza Mapiri, nkhalango komanso madambo ali mbulanda. Anthu adagwetsa mitengo ndi kuotcha makala. Koma lero nkhani yasintha. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Pangonopangono boma la Mwanza layamba kuvala, kubisa kusambuka kwake komwe kudadza pootcha makala. +Pulogalamu yolimbana ndi kusintha kwa nyengo yomwe ikutchedwa Enhancing Community Resilience Programme (ECRP) ndiyo ikusintha maonekedwe a bomalo komanso maboma ena. +Bungwe la Centre for Environmental Policy and Advocacy (Cepa) ndi lomwe labweretsa kusinthako. +Pulogalamuyi imalimbikitsa anthu kuti atsatire njira zosiyanasiyana zomwe zingawatukule uko akusamala nkhani zachilengedwe. +Alibe nthawi yootcha makala: Kheli ndi mkazi wake kutulutsa mbuzi Mwa zinthuzi ndi kuchita ulimi wa ziweto, wa kumunda, kugwiritsa ntchito mbaula zamakono, kuchita bizinesi, kutsatira njira zamakono zakalimidwe monga mtayakhasu komanso kulowa magulu obwereketsana ndalama banki mkhonde. +Amene akuyanganira momwe pulogalamuyi ikuyendera paboma ku bungwe la Cepa, Stephen Chikuse akuti ngati aliyense ali ndi chochita, nkovuta kuti mitengo isakazidwe. +Anthu alibe zochita, alibe popezera ndalama. Kungowauza kuti siyani kudula mitengo si zimveka. Ndi bwino kuwapezera chochita monga tikuchitira, adatero Chikuse. +Izi zasintha mabanja ambiri. Pakhomo pa James Kheli wa mmudzi mwa Sudala kwa Senior Chief Kanduku tsopano ndi pa mwana alirenji. +Nzeru za Cepa, lero Kheli ali ndi mbuzi 10, wayamba kukolola matumba 50 a chimanga kuchoka pa 15. Kheli ndi banja lake wabzala mitengo 300; akupanga ulimi wa mleranthaka komanso ali ndi munda wa chinangwa momwe akupha ndalama. +Ndikulipirira mwana wa folomu 3 ndipo pa telemu ndi K20 000. Ndamanga nyumba ya malata, ndagula wailesi komanso mpando wa pamwamba, adatero Kheli. +Nthawi yopanga makala monga ankachitira kale alibe, ndipo nthawi zonse amakhala kumunda, kubusa komanso banja lake limakhala kumsika kugulitsa mandasi momwenso akupha ndalama. +Monga akufotokozera mkazi wake Sineliya, kale amadalira makala koma lero nkhani idasintha. Kale, timapeza ndalama pootcha makala. Lero tili ndi njira zambiri zopezera ndalama, adatero iye. +Pulogalamu ya ECRP idakhazikitsidwa ndi Christian Aid komanso Concern Universal (Discover) koma thandizo la ndalama limachoka ku UK, Irish ndi boma la Norway. K21 biliyoni ndiyo idaikidwa. +Nkhani ya Kheli ndi chitsanzo chabe cha zomwe zikuchitikanso mmaboma a Nsanje, Chikwawa, Mulanje, Thyolo, Mwanza, Machinga, Balaka, Salima, Dedza, Kasungu ndi Karonga komwe CEPA ikugwiramo ntchito. +Luso la mpira ndilo lidandidolola Sabata zitatu zapitazo Sindi Simtowe adamanga ukwati ndi Ardron Msowoya, mnyamata yemwe akugwira ntchito ku Inde Bank. Kwa iwo amene amadikirira pa Sindi, pepani, mtima wa njoleyi wasankha wokha. +Kodi Sindi, katswiri womwetsa zigoli mtimu ya Malawi Queens, adakumana bwanji ndi wachikondi wake? Ardron akuti lidali tsiku lomwe adasiya ntchito yake ya mbanki ulendo ku BYC kukaonera njoleyi ikudoda osati masewero. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Sindi ndi Ardron tsopano ndi thupi limodzi Iye akuti wakhala akuwerenga munyuzipela za luso la Sindi kotero adaganiza zoti akadzionere yekha momwe namwaliyu amachitira. +Iye adatchera mafainolo a chikho cha OG Issa pamene timu ya Sindi, Tigresses, inkakwapulana ndi Diamonds. Ndiyetu ati udalipolipo. +Ardron atangofika pabwalopo, akuti adafunsa anthu kuti amulozere Sindi. Atandilozera kuti Sindi ndi uyo, ndidamuitana ndi kumupatsa moni. Sindidathe nthawi chifukwa amayenera alowe mbwalo koma akadandipatsa nthawi yaitali, ndimafuna ndipemphe nambala yake pomwepo. +Masewero atayamba, Ardron adasangalala ndi ntchito za Sindi. Akuti amati akadumpha, kuthamanga, kuchinya zigoli, mtima wa Ardron udakanika kudzigwira ndipo adakalephera kugona. +Pakutha pa sabata zitatu adali atapeza kale nambala ya Sindi ndipo mu May 2014 macheza sadachedwe, koma apo akuti amangocheza ngati munthu ndi mnzake. +Mu August 2014 ubwenzi udayamba. Koma kuti nditulutse Chichewa zidavuta, zimaonetsa kuti aliyense amafuna mnzake koma woyambitsa amasowa, adatero Ardron. +Mu June ndidamulembera uthenga wapafoni, koma sadayankhe, ndiye ndidamulemberanso wina kuti darling why are you not responding? chiyambi cha ubwenzi wathu chidatero, adatero mnyamatayu, amene wachita kulowola Sindi. +Ukwati udali pa 6 August ku Red Cross Church of Christ mumzinda wa Blantyre. +Makuponi adza ndi misonzi Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) komanso alimi ena apempha boma kuti likonzenso ndondomeko ya feteleza wotsika mtengo. +Pempholi ladza pamene zadziwika kuti kampani zimene zidapatsidwa mwayi wogulitsa alimi feteleza zikulephera kufikira madera onse komanso kuti mitengo yawo ndi yoboola mthumba. +Clara Nyandula wa ku Bamba kwa T/A Phambala mboma la Ntcheu wakhala akugulira feteleza wake pasukulu ya Matchereza chiyambireni ndondomeko yotsika mtengoyi. Pasukulupa akuti pamafika feteleza wa midzi 20 ya mwa T/A Phambala. Chaka chino akuti feteleza sadafike. +Banda kutha mtunda atagula feteleza Chimanga chafika popota, koma feteleza sitinagule. Pachifukwachi, tidaganiza zopita mboma la Balaka komwe tidakagula. Tidauzidwa kuti thumba ndi K7 000 la makuponi koma kukafika uko tagula thumba pa mtengo wa K12 000, adatero Nyandula. +Kuchoka mboma la Balaka kupita ku Ntcheu, thumba limodzi akuti amalipira K1 300. Zonse akuti zimalowa K14 000 kuti thumba likafika mmadera awo. +Zandiwawa kwambiri, sindidayembekezere kuti zifika pamenepa, ndi bwino ndondomeko ingotha chifukwa sindidaone ubwino wake, adatero mlimiyu. +Naye Frank Banda wa mmudzi mwa Namkumba kwa Senior Chief Somba mboma la Blantyre akuti nthawi zonse amagula feteleza pa Mpemba koma chaka chino feteleza sadafike. +Banda, amene tidamupeza mchikhamu cha ofuna kugula feteleza kukampani yogulitsa feteleza ya Optichem mumzinda wa Blantyre, adati ndondomeko ya chaka chino ndi yozunza alimi. +Ndinabwera kuno kuti ndidzagule matumba awiri omwe ndi K14 000, koma kudabwa akundiuza kuti thumba limodzi ndi K8 500, adatero iye. +Nako ku Zomba zasokonekera. Khansala wa wodi ya Mtungulutsi ku Zomba Lisanjala, Wilson Likusa, wati wodi yake muli anthu 2 000 amene adalandira makuponi koma matumba 200 okha ndiwo adafika. +Nzachisoni, chifukwa ngakhale mtengo wa thumba la feteleza ndi K11 000 komanso kuti ugule ukuyenera udutsire mwa munthu wina, adatero iye. +Senior Chief Kabunduli ya mboma la Nkhata Bay yati mavuto a chaka chino aposa a zaka zonse ndipo ngati boma silisamala zinthu zipitirira kuipa. +Tingolakwapo apa, tatopa ndi kudikira feteleza. Sitikudziwa kuti titani chifukwa madandaulo athu sakumveka. Alimi sadagule feteleza mpaka lero pamene chimanga chikupota, ndi zoona izi? adafunsa Kabunduli. +Izi zakhumudwitsa mkulu wa bungwe la Farmers Union of Malawi, Alfred Kapichira Banda yemwe wati alimi sangapeze phindu ngati boma silichotsa zotsamwitsazi. +Iye adati: Alimi ambiri sadagule feteleza. Ku Dowa, Kasungu mpaka Salima alimi akudandaula nkhani yake yomweyi. Komanso ku Dowa alimi ena akugula feteleza pa K24 000 thumba limodzi. +Uku ndi kupha alimi, palibe tsogolo ndipo tikupempha boma kuti lithamange kumva mavuto amene alimi akukumananawo ndipo akonze zinthu zisadavutitsitse, adatero Banda. +Mneneri wa unduna wa zamalimidwe, Hamilton Chimala, wati ndondomekoyi yabwera moyeserera kaye ndipo zomwe akufuna ndi kuthana ndi chinyengo. +Tidagwirizana kuti kampanizo zikwanitsa kufikira alimi, ndiye ngati nzoona kuti alimi ena mpaka lero sadagule feteleza chifukwa akumusowa, ndiye ndi zachisoni, adatero Chimala pamene adati unduna wawo uwunguza zotsamwitsa zonse. +Boma lidasintha ndondomeko ya zipangizo zotsika mtengozi pamene lidaika K15 000 pathumba lililonse lomwe mlimi agule ndi koponi. +Thumba lililonse, boma lidaikapo K15 000. Kusonyeza kuti mlimi azigula thumbalo motsika mtengo ndi kuponi ndipo ifeyo tidzapatsidwa kuponiyo ndikulipira kampani yomwe mlimiyo adakagula feteleza wake. +Izi zikusonyeza kuti mitengo izikhala yosiyana, zili kwa mlimi kusankha komwe akufuna kukagulira feteleza wake, adaonjeza. +Mpendadzuwa sulira madzi ambiri Mpendadzuwa ndi imodzi mwa mbewu zimene alimi angapindule nazo. HOLYCE KHOLOWA adacheza ndi Maxwell Chimombo wa mmudzi mwa Cedrick kwa Ngwelero ku Zomba amene akulima mbewuyi. Adacheza motere: Kodi mbewu ya mpendadzuwa imalimidwa bwanji? Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Choyamba mlimi amaunga mizere yokula ndi kutalikana ngati ya chimanga. Kachiwiri, mlimi amayenera kukhala ndi mbewu yabwino osati yobwafuka kapena ya matenda kuopera kuti ingavute kumera. Akatero, mlimi azingodikira mvula. +Chimombo kusankha mpendadzuwa kuti akabzale Kodi mpendadzuwa umabzalidwa ndi mvula yake iti? Mpendadzuwa timabzala kawiri wina timabzala limodzi ndi chimanga mvula yoyamba ija ikangogwa pamene wina timabzala pakadutsa mwezi ndi theka chibzalireni mbewu zina zija chifukwa sumafuna madzi ambiri. +Nchifukwa chiyani mpendadzuwa sumafuna madzi ambiri? Mpendadzuwa umene wabzalidwa ndi mvula uja ukamakololedwa wambiri umakhala mphwepwa chifukwa umakhala kuti udamwa madzi ambiri ali mmunda pamene wabzalidwa kachiwiri uja umakhwima mvula ikadukiza zimene zimachititsa kuti nthangala zake zikhale zangwiro zimene sizivuta malonda pa msika. +Mwachitsanzo, mlimi amene wabzala mpendadzuwa ndi mvula yoyamba akhoza kukolola matumba 20 koma akamazapeta akhoza kutsala ndi matumba 14 chifukwa chimachulukitsa matumbawo ndi mphwepwa pamene mlimi amene wabzala kachiwiri akhoza kukololanso matumba 20 koma akapeta mpendadzuwao akhoza kutsala ndi matumba 19 choncho mpendadzuwa wabwinoyu ndi wachiwiri. +Mwachitsanzo, chimanga changa ndinabzala mu November 2016 koma pano ndili pakalikiliki kulima komanso kusankha mbewu chifukwa mpendadzuwa ndibzala kumapeto kwa January uno kapena kumayambiriro kwa February. +Kodi mpendadzuwa mumabzala bwanji? Timabzala motalikana masentimita 75 phando lililonse komanso pa phando pamayenera kubzalidwa nthangala zosaposera ziwiri kuti mpendadzuwa ukule motakasuka bwino komanso kuti usamaphangirane chakudya cha munthaka. +Mbewuyi ikamera imayenera kumasamalidwa bwino makamaka poyipalira mwakathithi kuti mmundamo musakhale tchire limene ndi chiopsezo cha mbewu. +Dothi limene limakhala bwino kulimapo mpendadzuwa ndi lotani? Mpendadzuwa umachita bwino mdothi lililonse koma dothi la makande ndiye pachimake chifukwa limasunga madzi pamene dothi la mchengachenga mbewuyi imabereka mosisitika chifukwa madzi amalowa pansi msanga mnthaka kusiya mbewuyi pamoto. +Kodi mpendadzuwa umagwidanso ndi tizilombo kapena matenda? Mmmmmm pamenepo sindikudziwa bwinobwino chifukwa chiyambireni mpendadzuwa wanga sunagwidwepo ndi matenda. Chinsinsi changa ndi chakuti mmunda mwanga mumakhala mwaukhondo nthawi zonse zimene ndikukhulupirira zimathandiza kupewa matenda ndi tizilombo. +Ndi mavuto anji amene mumakumana nawo pa ulimiwu? Vuto lalikulu ndi misika yodalirika ya mpendadzuwa chifukwa kwathu kuno amatigula mpendadzuwa ndi mavenda. Kuipa kwa mavendawa ndi kwakuti iwowo ndi amene amatipangira mitengo. Nthawi zambiri mavendawa akafika amatiuza kuti malonda a mpendadzuwa sakuyenda bwino kumisika ikuluikulu mtauni choncho atigula pa mitengo yotsika. Ndiye chifukwa ife kumisika ikuluikuluko sitimakudziwa timangogulitsa pa mitengo imene mavendawo afuna. +Mwachitsanzo, mu 2016 alimi timafuna tikumagulitsa pa mtengo wosachepera K200 pa kilogalamu koma mavenda atafika kuno amatigula pa K170 zimene zinatiwawa kwambiri. +Vuto la kusowa kwa misikali mukuganiza lingathe bwanji? Tikupempha eni makampani komanso akuluakulu a zaulimi mdziko muno kuti abwere kwathu kuno adzadzionere okha mmene anthu tikulimira mpendadzuwa chifukwa kwathu kuno tiliko alimi ambiri komanso adzatipatse upangiri wa mmene tingamapezere misika yodalirika ya mpendadzuwa chifukwa mavendawa akutidyera masuku pamutu. +Anatchezera Ndikufuna sukulu Zikomo Anatchereza, Ndine msungwana wa zaka 19. Sindidakwatiwepo, ngakhale sukulu ndidaisiyira Fomu 1 zaka zutatu zapitazo. +Sukuluyo ndidasiya chifukwa chosowa ndalama chifukwa makolo anga adasiyana ndipo sangathe kundithandiza. +Padakali pano ndikugwira ntchito mnyumba ya munthu. Izi ndidapanga chifukwa anthu amandiuza kuti ndikwatiwe koma ine sindimafuna zimenezo. Ndimafuna kudzakwatiwa ntakonza tsogolo lowala. +Chikundivuta ndi nkhani imene ndili nayo patsogolo langa. Nditani kuyi tsogolo langa likhale lowala. +MN, Thyolo. +MN, Ndathokoza polemba uthenga wanh wogwira mtima. Ndihamike chifukwa cha luntha lanu pofuna maphunziro. Si asungwana ambiri amene ali paumphawi amene amaganiza momwe mukuchitiramu. +Si zoona kuyi kulowa mbanja ndiye kuthana ndi mavuto. Mwinanso kumakhala kuonjezera mavutowo chifukwa kumakhala kosavuta mwamuna kuzunza mkazi amene akumuona kuyi alibenso kolowera. +Popeza mwanena kuyi mukugwira ntchito, langizo langa likhoza kukhala lakuyi, simungagwiritseko gawo lina la ndalama zimene mukulandira polipira sukulu? Mutabwerera kusukulu, ngakhale mukugwira ntchito, zikhoza kuthandiza. Alipotu ambiri amene leto lino akuvhita bwino koma sukulu adaphunzira akugwira pakhomo la munthu. +Chofunika nkuwagoyokozera bwino abwana kapena adona anu kuti sukulu siyikulepheretsani kugwira bwino ntvhito pakhomo lawo. Zabwjno zonse. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Nsanje yakula Anatchereza, Poyamba ndithokoze chifukwa cha kwanu kutithandiza pamavuyo amene timakumana nawo. +Ndili ndi chibwenzi chimene chakhala chikunena kuti chidzandikwatira mu 2017. Koma akangomva kankhani kakangono, amakhumudwa ndipo amathetsa chibwenzi. +Izi zakhala zikuchitika kanayi konse. Nkhani yalero ndi ya pa Facebook, pomwe mnyamata wina wandiyamikira momwe ndikuonekera lachithunzi china. +Bwenzi langayo akuchita nsanje kuganiza kuti ndijuyenda ndi mnyamatayo koma ayi. +Chonsechotu ndidamupatsa password yanga kuti aziona ngakhale mauthenga anga obisika. Zikundisowetsa mtendere nditani. +GK, Mulanje. +GK, Mwamunayo wamukonda, mpaka kumupatsa password! Chikondi chiyenera khbwezeredwa. Kodi iyeyo adakipatsa password yake? Ena amati nsanje ndi maziko a chikondi koma nsanje ina inyanya. Nsanje ina I asonyeza kuti wochita nsanjeyo ndi kamberembere chifukwa amaganiza kuti zimene amachita ndiye kuti enanso akateto zili choncho. +Mwachitsanzo, mwina iye naye amauza asungwana ena kuti zithunzi zawo zikumusangalatsa nchokinga chakuyi awakope tsono akuona ngati mnyamata aliyense akakuuza chimodzimodzi ndiye kuti nayenso akufuna kukukopa. Pomwe si zili choncho. +Atenge basi ndani? Matimu a Nyasa Big Bullets ndi Mighty Be Forward Wanderers Lolemba akhala akukumana pampikisano wa Basi Ipite Soccer Fiesta wolimbirana minibasi ya K25 miliyoni pa Kamuzu Stadium mumzinda wa Blantyre. +Mkulu wa Luso TV Dick Juma Lachinayi adati basiyo, imene idafika mdziko muno Lachinayi, ipitirira kusungidwa ndi bungwe la Football Association of Malawi (FAM) mpaka wopambana apezeke. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ilowera kwa ndani?: Wachiwiri kwa wapampando wa Bullets (kumanzere) Austo Kasito ndi Christo Kananji wachiwiri kwa mlembi wa Manoma Basi ndi imeneyi yafika lero ndipo mawa (Lachisanu) ikaperekedwa mmanja mwa FAM kuti ayisunge, adatero Juma. +Iye adati adasankha matimuwa kaamba ka mavuto a mayendedwe omwe ali nawo ndipo akufuna kupereka mwayi woti opambana adziombole kumavutowa. +Musasusukire dzombeunduna Ngakhale dzombe limaononga mbewu, kwa anthu ena ndi ndiwo zankhuli. Koma unduna wa zamalimidwe, ulimi wamthirira ndi chitukuko cha madzi wachenjeza kuti anthu asasusukire dzombe lomwe lapoperedwa mankhwala. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Dzombe lidagwa ndi kusakaza mmera wamthirira ndi nzimbe mmadera a chigwa cha Shire, nkhani yomwe yadula chiyembekezo cha mpumulo pankhani ya njala. +Mlembi wamkulu muundunawu, Erica Maganga, Lachitatu adati ngakhale mankhwala omwe akupoperedwawo sapha dzombe, akhoza kukhala ndi zotsatira zoipa pamoyo wa munthu. +Koma Lachinayi nyuzi ya Nation idayankhula ndi mneneri wa kampani yopanga shunga ya Illovo ku Ntchalo mboma la Chikwawa, Irene Phalula, yemwe adatsimikiza zoti kampaniyo idapopera mankhwala a fipronil omwe adapha dzombe miyandamiyanda patatha maola 24 chipopereni. +Maganga: Musadye dzombe lopopera Mosakaika anthu ena poona dzombe lakufalo amangoti laponda lamphawi, ndiwo zapezeka, osadziwa kuti akuika miyoyo yawo pachiposezo. +Vuto ndi lakuti anthu ambiri amakonda zinthu zobwera mosavuta pomwe ena amaona ngati apeza mpamba wa bizinesi ndiye, ngati unduna, tikunenetsa kuti dzombeli si labwino kudya, ayi, adatero Maganga. +Iye adati zomwe achita a kampani ya Illovo nzotamandika chifukwa kulilekerera, dzombe likadakhoza kufalikira mmadera ambiri ndi kuononga mbewu ndi zomera zina. +Mfumu yaikulu Malemia ya ku Nsanje yati nkofunika kumva malangizo a akatswiri monga a kuunduna wa zamalimidwe kuti anthu asaononge miyoyo yawo kapena ya anthu ena. +Dzombe ndi mtundu wa ziwala zomwe zimayenda mchigulu ndipo likangofika pamalo limaononga zomera moti kulilekerera likhoza kukhala gwelo la njala ndi umphawi waukulu mdziko muno. +Dzombeli lidaoneka sabata yatha ku Bangula mboma la Nsanje komwe lidayambira utumiki wake wosakaza mbewu, makamaka chimanga chamthirira mmahekitala 30. +Sabata ino, dzombeli lidafika mboma la Chikwawa komwe mkulu wa zamalimidwe, Ringston Taibu, komanso mneneri wa kampani yopanga shuga ya Illovo ati laononga mahekitala 405 a nzimbe. +Phalula adati kampani ya Illovo ili kalikiriki kupopera mankhwala mminda ya nzimbe koma adati mankhwalawo sapha dzombe koma kungolifoola kuti lisiye kuwonongako. +Dzombeli lidafika usiku wa Lolemba ndipo lidagwira munda wa mahekitala 50 a nzimbe lisadalowerere mmunda wina wa mahekitala 120. Kuchoka apo lidakagwiranso munda wina wa mahekitala 115 kufupi ndi munda womwe tikuchitira ulimi wamthirira, adatero Phalula. +Iye adati usiku womwewo kampani itaona kuti dzombelo likhoza kulowerera kumunda wamthirirawo, idayamba kupopera mankhwala koma adati kuwonongeka kwa nzimbeko sikusokoneza makololedwe. +Mtembo usagone panoAchipatala Pasathe tsiku mtengo wanu musadadzatenge. Uthenga omwe a zipatala za Rumphi ndi Machinga akuuza anthu chifukwa cha kuonongeka kwa malo wosungira mitembo pachipatalapo. +Pachipatala cha boma ku Rumphi, zaka ziwiri zatha malo osungira mitembowa atasiya kugwira ntchito pamene ku Machinga, miyezi itatu yatha malowa atasiya kugwira ntchito. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Jobe: Boma lichitepo kanthu Izi sizidakomere anthu amene amagwiritsa ntchito zipatalazi amene anena kuti boma ndi mabungwe alowererepo kuti zotere zisinthe. +T/A Nyambi ya mboma la Machinga akuti pakhala povuta kuti anthu azikatenga thupi la malemu tsiku lomwelo chifukwa palibe amene amakonzekera maliro. +Ambiri tikukhala kutali ndi chipatalachi. Zovuta zikagwa timadalira kuti pathe tsiku kuti tipeze mayendedwe. Tikuvutika chifukwa kuchipatalako kulibe galimoto zokwanira kuti azikatisiyira zovuta pakhomo pathu, adatero Nyambi. +Mneneri wa chipatala cha Machinga, Clifton Ngozo akuti sangachitire mwina chifukwa ngati angasunge thupi kwa nthawi ndiye kuti lingathe kuonongeka. +Kudachitika ngozi, tidasunga matupi amene amakha magazi. Padatha masiku awiri kuti matupiwo apite kukaikidwa koma kudali fungo loipa. Ndiye sizithekanso kuti tisunge mtembo pokhapokha malowa atakonzedwa, adatero Ngozo. +Iye adati ngati atapitirira kumagoneka mitembo ndiye kuti zingabweretse zotsatira zoipa monga matenda kwa amene akugwira ntchito kumalowa. +Poyamba timasunga mitembo kwa masiku oposa awiri kapena atatu koma akamadzatenga mtembowo umakhala uli bwinobwino. Panopa sizingathekenso chifukwa malowa aonongeka. +Panopa uthenga omwe tikuuza anthu amene amagwiritsa ntchito malowa ndikuti sitikwanitsanso kuti matupi azigona kumeneku. Zovuta zikachitika atha kusunga koma asagone chifukwa aonongeka, adatero Ngozo. +Kuchipatala cha Rumphi, anthu adasiya kugoneka mitembo chifukwa cha kuonongeka kwa malo osungira mitembo. +Mneneri wa chipatalachi Bwanalori Mwamlima akuti malo osungira mitembo adaonongeka zaka khumi zapitazo koma akhala akukonzetsa mpaka 2015. +Panopa sitingakonzenso, chifukwa pena tikakonza sichimachedwanso kuonongeka. Apapa zavuta ndipo tasiya kugoneka mitembo chifukwa ikumaonongeka, adatero Mwamlima. +Iye akuti vuto nkuti zipangizozi zakhalitsa. Ndikakumbuka bwino, zipangizozi zidaikidwa mma 1976, zakhala zikugwira ntchito mpaka lero, adatero Mwamlima. +Izi zakhumudwitsanso mkulu wa bungwe loona za umoyo la Malawi Health Equity Network (Mhen) George Jobe amene wati aphungu a Nyumba ya Malamulo akuyenera aikambirane pamene akhale akukumana. +Amene adamanga nyumba yachisoni adali ndi cholinga ndipo adaona kufunikira kwake. Izi si zoona kuti mpaka malowa asiye kugwira ntchito chifukwa talephera kuwakonza. +Palibe amene amayembekezera maliro pamene wapita kuchipatala. Ndiye simunganene kuti maliro akangochitika basi munyamule, adatero Jobe. +Ku Salima nakonso akhala akukumana ndi mavuto omwewa koma pano zidayenda pamene malo osungira mitembowo adakonzedwa. +T/A Mwanza wa mbomali akufotokoza. Tidakumana ndi mavutowa koma panopa zinthu zilibwino pachipatalachi chifukwa adakonza, adatero Mwanza. +Ndale pamaliro nchitonzo Katswiri pa zachikhalidwe, Emily Mkamanga wati zomwe zakhala zikuchitika pa miyambo ya maliro mdziko muno ndi belu lozindikiritsa kuti andale si ofunika kuwapatsa mpata wolankhula pa miyamboyi. +Mkamanga adanena izi pamene mpungwepungwe udabuka pamaliro a mayi a Senior Chief Lukwa ku Kasungu pomwe phungu wa deralo wa chipani cha MCP Amon Nkhata adalandidwa chimkuzamawu ndi gavanala wa DPP Osward Chirwa pomwe mmodzi mwa akuluakulu a DPP Hetherwick Ntaba adathothedwa pamaliropo. Izi zachititsa mfumu yaikulu ya Achewa ku Zambia, Malawi ndi Mozambique Kalonga Gawa Undi alembere mafumu a kuno kuti afotokoze chimene chidatsitsa dzaye kuti mpungwepungwewo ugwe. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mmbuyomu, Paramount Lundu idawoozedwa pamaliro a mfumu Kabudula pomwe adanena kuti chipani cha MCP sichingalamulirenso dziko lino. Ndipo kudalinso mpungwepungwe ku zovuta za anthu amene adamira panyanja ku Jalawe mboma la Rumphi pomwe achipani cha DPP adakhambitsana ndi a Livinstonia Synod ya CCAP. +Mkamanga adati nthawi ya maliro, anamfedwa amakhala mchisoni ndipo khamu la anthu omwe limasonkhana limadzakuta ndi kukhuza malirowo osati kudzamvera kampeni kapena mfundo za ndale. +Sindidziwa kuti amaganiza bwanji. Nthawi yoti mnzako akulira, iwe sungasandutse guwa lochitirapo kampeni. Kuli bwino andalewo asamapatsidwe mpata nkomwe woti alankhule pamaliro, adatero iye. +Iye adati zimamvetsanso chisoni kuti anthu ena amaveka maliro dzina la chipani pomati maliro awa ndi achipani chakuti pomwe pachilungamo chake, chipani chilibe maliro, maliro amakhala a banja. +Chilowereni chaka chino chokha, malilo angapo makamaka a anthu akuluakulu kapena odziwika akhala akusokonekera chifukwa cha zolankhula za andale. +Likodzo limatha magazi mthupi Likodzo ndi matenda amodzi amene akapanda kuzindikiridwa msanga akhoza kupha munthu chifukwa amayamwa magazi. +Michael Luhanga amene ndi katswiri pa matenda a likodzo kuofesi ya zaumoyo ku Zomba adati likodzo limafala ngati munthu amene ali ndi likodzolo wakodzera mmadzi ndipo nkhono zimene zimanyamula tizilombo ta nthendayi tikhudzanso munthu wina amene alibe likodzo. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndi bwino kupewa kukodzera mmadzi kapena kuchita chimbudzi patchire chifukwa madzi a mvula akakokolola zimenezi ndi kukathira mumtsinje ndiye kuti anthu onse amene akugwiritsa ntchito madziwo ali pachiopsezo chotenga likodzo, adatero Luhanga. +Luhanga: Nthawi ya mvula ndi yofunika kusamala Malinga ndi Luhanga likodzo lilipo la mitundu iwiri: la mmatumbo komanso la mchikhodzodzo. +Zizindikiro zooneka ndi maso kuti munthu ali ndi likodzi ndi kukodza timadontho ta magazi makamaka akamamaliza kukodza, adatero Luhanga. +Kupatula kutha magazi mthupi, likodzo limachititsanso kuti ana azikula monyentchera, ana amakula opanda nzeru, kusabereka kwa amayi, khansa ya khomo la chiberekero, kutupa kwa kapamba ndi chiwindi komanso kudzadza kwa madzi mmimba. +Ndi bwino kuti anthu akaona kuti akukodza magazi azithamangira kwa alangizi a zaumoyo kudera lawo kapena kuchipatala matendawo asanayale maziko mthupi mwawo, adatero Luhanga. +Katswiriyu adati anthu amene ali pachiopsezo chachikulu chotenga likodzo ndi ana chifukwa amakonda kusewera mmadzi akuda a mvula komanso anthu amene amalima mpunga kumadambo ndi mbewu zina ndi amene ali pachiopsezo chotenga likodzo. +Tikulangiza anthu kuti azigwiritsa ntchito zimbudzi akafuna kudzithandiza chifukwa kukodza kapena kuchita chimbudzi paliponse ndi koopsa masiku ano a mvula, adalangiza Luhanga. +Iye walangizanso kuti likodzo ndi lochizika chifukwa wodwala amapatsidwa mankhwala a praziquantel amene amathaniratu ndi likodzo mthupi. +Mtima pansi, makuponi akubwera Boma lati anthu omwe chiyembekezo chawo chili pazipangizo zaulimi zotsika mtengo za sabuside, asataye mtima ndipo achilimike kukonza mminda mwawo kaamba kakuti makuponi ogulira zipangizozi afika sabata ikudzayi Lolemba. +Chilimbikitsochi chadza pomwe anthu adali ndi nkhawa kuti mvula yayandikira komanso madera ena yagwa kale mwa ndii koma tsogolo la makuponi ogulira zipangizo silimaoneka bwinobwino. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Fisp fertiliser and seed will be handled by private traders this year Mvulayi yagwa mmadera ena mzigawo zonse kuyambira sabata zitatu zapitazo ndipo pomwe anthu ena ali jijirijijiri mminda mwawo, anthu ena amadandaula kuti mwina mwayi wogula zipangizozi ukhoza kudzafika mmera utakwinimbira. +Si zongoganiza ayi, taziwonapo mmbuyomu kuti pomwe zipangizo zikufunika, kumisika kulibe kapena makuponi sadafike ndiye umayamba ntchito nkudzakhumudwa pambuyo, adatero Ammon Yesani Bakulo, mmodzi mwa alimi omwe akuyembekezera kulandira nawo makuponi kwa Chiseka mboma la Lilongwe chaka chino. +Koma nduna ya zaulimi, mthirira ndi chitukuko cha madzi, George Chaponda, wati nkhawayi njopanda mtsitsi kaamba koti mkati mwa sabata ikudzayi, makuponi ayamba kufika ndipo azigawidwiratu. +Ndikunena pano, makuponi adindidwa kale moti sabata yamawayi akhala akufika ndipo nthawi yomweyo azigawidwa kuti anthu ayambe kugula zipangizo. Sitikufuna kuti munthu adzadandaule patsogolo, ayi, adatero Chaponda. +Mndondomeko ya chaka chino muli kusintha kungapo komwe Chaponda wati kuthandiza kupititsa patsogolo cholinga cha pologalamu ya sabuside. +Kwina mwa kusinthaku ndi kukhazikitsa mitengo yatsopano ya makuponi, kutsitsa chiwerengero cha anthu omwe apindule mupologalamuyi, komanso kupereka kontirakiti kwa makampani abizinesi kuti agulitse nawo zipangizozi. +Kubwera kwa makampani abizinesi ndi kumodzi mwa kusintha komwe kuthandize kwambiri ndipo kupangitsa kuti zipangizo zotsika mtengo zizipezeka pafupi ndi anthu komanso chifukwa cha mpikisano, mitengo isanyanye poti aliyense azifuna kugulitsa, adatero Chaponda. +Mupologalamu ya chaka chino, mtengo wa kuponi ya feteleza wokulitsa ndi wobereketsa uli pa K15 000 pomwe mbewu za chimanga papaketi ya 5kg kuponi yake ili pa K5 000 ndipo mbewu zamtundu wa nyemba zolemera 2kg mpakana 3kg kuponi yake ili pa K2 500. +Chaponda adati mitengoyi ndi yomwe boma likuwonjezera pa mlimi, osati mitengo yogulira kumsika. +Mwachitsanzo, ngati thumba la feteleza lili pa K18 000, ndiye kuti boma laperekako K15 000 ndipo K3 000 yotsalayo apereke ndi mlimi, adatero Chaponda. +Malingana ndi malipoti a zanyengo, chaka chino, mvula ikhoza kugwa bwino moti unduna wa zamalimidwe, mthirira ndi chitukuko cha madzi ukulimbikitsa alimi kuti alimbikire ntchito za mminda. +Ndalama zaperewera mmagawo ofunikira Ngakhale maunduna a zamalimidwe, umoyo ndi maphunziro alandira ndalama zochuluka kwambiri mundondomeko ya momwe boma liyendetsere chuma kuyambira pa 1 July chaka chino mpaka pa 30 June chaka cha mawa, akadaulo a nthambizi ati ndalama ndi zochepa kupititsa patsogolo ntchito za maundunawa. +Izi zikudza pomwe aphungu a Nyumba ya Malamulo alowa mmilaga kukambirana ndondomeko ya zachuma imene nduna ya zachuma Goodall Gondwe adapereka pa 19 May. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ana ena akuphunzira mzisakasa ngati izi Mwachisanzo, unduna wamaphunziro wapatsidwa K235 biliyoni, koma mkulu wa bungwe loona zamaphunziro la Civil Society Education Coalition (CSEC) Benedicto Kondowe wati kusalana pamaphunziro kupitirira mdziko muno chifukwa ndalamazo sizikwanira kuthetsa mavuto. +Kondowe adati ndalama zoonjezera zikufunika kuti ana akumidzi apeze maphunziro abwino okweza umoyo wawo. +Zikungooneka zochuluka koma magawo othandiza kuti tikhale ndi maphunziro abwino sadaganiziridwe. Palibe dongosolo lolemba ntchito aphunzitsi 10 000 a msukulu za pulaimale omwe boma lidaononga ndalama kuphunzitsa. Silidaikenso ndalama zoonjezera malipiro aphunzitsi omwe adakwezedwa maudindo. Mabajeti anayi apitawo boma limaika K300 miliyoni yothandizira kukhazikitsa koleji ya aphunzitsi a ana olumala koma chaka chino ayi, adatero Kondowe. +Popereka ndondomekoyi Gondwe adati unduna wa zamaphunziro walandira ndalama zochuluka polingalira kuti ukuyenera kuonjezera zipangizo msukulu za ukachenjede ndi zophunzitsa maluso osiyanasiyana. +Iye adati kupatula apo, undunawu ukuyenera kuonjezera ndi kukonza zofunika msukulu zosiyanasiyana kuti maphunziro apite patsogolo mdziko muno. +Tikufunitsitsa kuti mdera la phungu aliyense mukhale sukulu yoyendera ya sekondale ya zipangizo zonse zoyenera monga nyumba yophunzirira sayansi ndi kuwerengeramo mabuku, adatero Gondwe. +Koma Kondowe adati ndalama yomangira nyumba za sayansi ndi zokwanira msukulu 100 zokha zomwe sizifikira ophunzira a kumidzi ndi maphunzirowa. +Iye adati boma likuyenera kukwaniritsa ndondomekoyi chifukwa chaka chatha lidalonjeza kumanga nyumba zowerengeramo zomwe silidamange mpaka pano. +Mmodzi wa akatswiri a zamalimidwe mdziko muno Tamani Nkhono-Mvula adati ndalama ndi zochepa chifukwa akatswiri adayerekeza K250 biliyoni kapena K300 biliyoni kuti ulimi uchite bwino mdziko muno. Unduna wa malimidwe udapatsidwa K192 biliyoni pa ndondomeko ya chaka chinoyo. +Ndizochepa, undunawu ulibe ogwira ntchito 50 pa 100 ofunikira.Gawo la ulangizi likufuna ndalama zambiri chifukwa limagwira ntchito ndi alimi mmidzi.Ndalamazi sizikwanira chifukwa zofunika za unduwa ndi zambiri, iye adatero. +Mvula adaonjezera kuti ulimi mdziko muno ukhonza kupita patsogolo ngati boma ndi mabungwe atagwiritsa ntchito moyenera ndalama zomwe zili mgawoli. +Ndalama zambiri sizigwira ntchito yake.Malingana ndi mavuto a zachuma, bajeti yachepa koma zochoka ku mabungwe ndi zambiri zomwe zingathandize kuthetsa njala mdziko zitalondolozedwa bwino, adatero Nkhono-Mvula. +Mkulu wa bungwe loona umoyo wabwino wa anthu la Health and Rights Education Programme (HREP) Maziko Matemba adati aphungu ku mlaga wa zaumoyo ku Nyumba ya Malamulo adziwe kuti ndalama zopita ku zipatala za zingono komwe anthu mmidzi amapeza thandizo zachepa. +Boma likulingalira zoika aliyense ali ndi HIV pa ma ARV, koma bajeti ya mankhwala [K10 miliyoni] siyidakwere zomwe zikudzetsa nkhawa ngati ikwanire. Dziko lili mmigwirizano ndi mabungwe monga Global Fund komwe tikuyenera kupereka K11 biliyoni kuti chaka chamawa tilandire mankhwala a chifuwa chachikulu (TB) ndi ma ARV kuchoka pa K129 biliyoni, adatero iye. +Ngozi idazamitsa chikondi chathu Anthu adavulala, ena adataya miyoyo yawo. Koma kwa Joseph Chirwa ndi Towera udali mwayi kuti awiriwa akumane ndi kumanga woyera. +Lero ndi thupi limodzi, koma nkhani yano imaseketsabe akakumbuka za ngozi yomwe idachitika mu 2010 mboma la Zomba, iyo idali ngozi ya basi. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Towera adali mbasimo ndipo adavulala ndi kutengeredwa kuchipatala. Panthawiyo nkuti awiriwa atakumana kale ndi kupatsana manambala koma zolota kuti akapizana mawu a chikondi panalibe. +Joseph ndi Towera lero ndi banja Joseph yemwe akugwira ntchito kunthambi yoona za anthu olowa ndi kutuluka mdziko muno atamva kuti Towera wapanga ngozi, adakhudzidwa ndipo samati waimbanso liti foni komanso kukamuona. +Chifukwa choimbaimba, tidakhala pachinzake kwambiri, kenaka tidayamba kufunana, adatero Joseph pamene adamudikira Towera achire kaye kuti nkhani yachikondi ilowe mbwalo. +Joseph akuti pamene izi zimachitika nkuti awiriwa atakumana kale ku Masintha CCAP komwe onsewa amapemphera. +Apo Joseph nkuti ali mtsogoleri wa achinyamata, Towera adali membala wagulu la maimbidwe. +Komabe panthawiyo zoti angadzakhale thupi limodzi sizimadziwika. Zidatengera ngozi ya ku Zomba kuti zenizeni zioneke. +Mu 2012 Towera adali atachita, ndipo Joseph adaponya Chichewa. Pounguza chikondi chomwe mtsogoleriyu adachionetsa pa nthawi ya matenda, Towera sadazengereze koma kuvomera. +Joseph ndi oopa Mulungu. Wachikondi komaso wosamala. Iye amalingalira mwakuya ndipo ndidapeza tsogolo langwiro mwa iye, adatero Towera. +Naye Joseph adabwekera kuopa Mulungu kwa njoleyo: Towera ndi oopa Mulungu, ali ndi maonekedwe abwino ndipo ndisanamepo mkazi wanga ndi nthwani. +Ukwati udali pa 31 October 2015 ku Masintha CCAP ndipo madyerero adali ku ku Lilongwe Golf club. +Nkhanza zapolisi zanyanya Ophunzira 24 a kusukulu za ukachenjede apereka maina awo ku bungwe la maloya la Malawi Law Society (MLS) za nkhanza zimene achitiridwa panthawi yomwe amachita zionetsero zokwiya ndi kukwera mtengo kwa fizi. +Iwo adachita izi MLS itawapempha kuti apereke mainawo potsatira nkhanza zimene apolisi adachitira ophunzirawo amene akwiya kuti fizi zakwera kuchokera pa K275 000 kufika pa K400 000. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Apolisi kuponda mwana akufuna kutolera mabotolo ku Kamuzu Stadium Nkhanzazo zidafika pambalambanda kwambiri ena atajambula pa vidiyo wapolisi wina ataomba khofi wophunzira wa chaka cha chinayi Mayankho Kapito, yemwe ndi mwana wa mkulu wa bungwe loona zaufulu wa anthu ogula la Consumers Association of Malawi (Cama) John Kapito. Kapito wati asumira apolisiwo. +Mtsogoleri wa ophunzira ku Chancellor College Ayuba James adatsimikiza kuti pofika Lachitatu chiwerengero cha ophunzira omwe adapereka maina awo adali atafika pa 24. +Talandiradi mainawo koma tikudziwa kuti chiwerengero chayenera kukhala chokwera kwambiri chifukwa ambiri apitapita mmakwawo. Nkovuta kuti uthengawu uwafikire, adatero James. +Chikalata cha MLS chidapempha ophunzira amene angakhale ndi umboni wa nkhanzazo kuti apereke maina awo. Ngakhale mneneri wa bungwelo Khumbo Soko adatsimikiza za ntchitoyo, adakana kuthirirapo ndemanga chifukwa ati akadali mkati mopeza mainawo. +Nthawi ya zionetsero za ophunzirawo, apolisi akhala akumenya ophunzirawo ndipo amangapo angapo pa zipolowe zomwe zakhala zikuchitika msukulu zomwe zili pansi pa University of Malawi (Unima). +Izi zili apo, mabungwe ena a zaufulu wa Amalawi ati nkhanza zankitsa kupolisi ndipo ati izi zikusemphana ndi zimene amalengeza kuti adasintha. +Sabata yatha, dotolo wodziwika bwino Dr Frank Taulo adalemba pa Facebook kuti adapeza apolisi akumenya anthu amene adawapeza akungoyenda mu Limbe mumzinda wa Blantyre nthawi itangokwana 6 koloko madzulo. +Nditawafunsa chifukwa chiyani amamenyera anthuwo, adandikuta. Nditawauza kuti ndine wakuti, sadalabadire ndipo adandionongeranso galimoto langa, adatero Taulo. +Posakhalitsapa, mwini malo ena a chisangalalo ku Chigumula mumzindawu, Sharat Gondwe adatinso apolisi adamumenya atabwera kudzatseka malo akewo, Pitchers Club. +Anthu ena amene tidacheza nawo ku Lilongwe nawo adasimba za nkhanza za apolisi. Gift Potani wa kumsika wa ku Area 24, Andrew Mwenye wa mumsika wa Tsoka komanso Alinafe Matthias wa ku Area 22 adanena kuti apolisi akumanga anthu kapena kuwakwapula kumene opanda chifukwa chenicheni. +Nthawi zina amapeza anthu malo omwera masanasana nkuwaphaphalitsa, ena kutengedwa osapatsidwa mpata wofotokoza zomwe akuchita, adatero Potani. +Si ana a sukulu kapena Amalawi wamba amene akudandaula za nkhanzazi. Nawo amayi oyendayenda ati amakumana ndi nkhanza za apolisi akagwidwa pantchito yawoyi. +Mneneri wa bungwe loyimilira amaiwa, Zinenani Majawa, adati pakati pa apolisi pali Chichewa choti Dzipulumutse kutanthauza kuti wogwidwayo apereke kena kake kapena akakhala mzimai asinthitse thupi lake ndi ufulu. +Apolisi akatigwira vakabu amati dzipulumutse wekha kutanthauza kuti akufuna ndalama ndipo ngati palibe amamumenya kapena kumugona mzimai popanda chitetezo chilichonse ndiye poti ndi wapolisi, kokanena kumasowa, adatero Majawa. +Mkulu wa bungwe la zaufulu la Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR) Timothy Mtambo adati apolisi akadaunika mofatsa magwiridwe awo antchito kuti pomwe akuteteza miyoyo ndi katundu, asamaphwanye ufulu wa ena. +Mneneri wa apolisi mdziko muno Nicholas Gondwa adaikira kumbuyo apolisi ndipo adati akugwira ntchito yawo potsata malamulo. Mawuwo adadza pomwe apolisi adalengezanso kuti akufufuza za wapolisi wothyapa khofi mwana wasukulu. +Tikafika poponya utsi okhetsa misozi ndiye kuti zionetsero zafika pa zipolowe pofuna kuteteza anthu amene sizikuwakhudza ndi katundu wawo. Komanso kumanga ena mwa anthuwo kumakhala kuziziritsa zipolowezo, adatero Gondwa. +Admarc isagulitse chimanga kunja Bungwe la Admarc lisatengeke ndi zakuti dziko lino likhoza kukolola chimanga chochuluka chaka chino nkugulitsa chimanga kunja padakalipano, mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a zaulimi la CisaNet Tamani Nkhono-Mvula watero. +Nkhono-Mvula adauza Tamvani pomwe Admarc ikulingalira zogulitsa chimanga chimene lidagula ku Zambia kumaiko a Kenya ndi Tanzania. Izi zadza pomwenso mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika atalamula asilikali kuti akhamukire kumalire a dziko lino ndi kugwira ofuna kugulitsa kunja chimanga mozemba. Lamulolo lidadza apolisi atagwira galimoto 17 zimene zimafuna kutulutsa chimanga mozemba. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Zina mwa galimoto zimene zidagwidwa Iye wati mmera omwe uli mminda usapereke chiyembekezo chabodza kuti Admarc igulitse kunja chimanga. +Njala ikadalipo. Zonse zidzadziwika bwino kafukufuku womaliza wa zokolola akadzatulutsidwa. Posakhalitsapa timasaka chimanga Amalawi atasauka ndi njala, choncho kuchigulitsa panopa kunja ndi chibwana cha mchombo lende, adatero Nkhono-Mvula. +Iye adati chimanga sichingasowe msika ngakhale mdziko momwe muno, koma phuma silingathandize konse. +Pamene boma lakhwimitsa chitetezo kuti chimanga chisatuluke, pakuyeneranso kukhala chitetezo momwe chimanga chikugulitsidwira mdziko momwe muno. Pali vuto lalikulu pamene chimanga chochokera kumwera chikukagwidwa ku Karonga, adatero mkuluyo. +Iye adatinso mpofunika kuti boma kudzera ku unduna wa za malonda kapena malimidwe azipereka ziphaso zapadera kwa anthu ofuna kuchita malonda achimanga. +Ndipo polankhula pomwe amakhazikitsa ntchito ya magetsi mmidzi, Mutharika adati ngakhale maiko a Kenya ndi Tanzania ati akufuna kugula chimanga kuchoka ku Admarc, salola kuti izi zichitike. +Zidachitikapo mmbuyomu kuti pamene tili ndi chimanga chochuluka tidachigulitsa ku Kenya koma chaka chotsatira kudali njala yadzaoneni mpaka kumakagulanso ku Kenya komweko, adatero Mutharika, nkupemphanso Amalawi kuti asagulitse chimanga chawo kwa mavenda koma kudikira misika ya Admarc itsegulidwe. +Wapampando wa nthambi yoyanganira ntchito za Admarc James Masumbu adati mapulani ogulitsa chimanga ku Tanzania ndi Kenya alipo koma akudikira kuti alimi akolole kaye. +Panopa, pologalamu yonse yaima chifukwa tikufuna tiyambe takolola kuti tiwone chakudya chomwe alimi akolole kuti tidziwe pomwe chitetezo cha dziko chilili kumbali ya chakudya kenako tidzapanga ganizo lenileni, adatero Masumbu. +Iye adati kugulitsa chimangachi sikuzungulira mutu koma kuti bungweli lili ndi ngongole yofunika kubweza ndipo ndalama zobwezera ngongoleyi zikhoza kupezeka msanga pogulitsa chimangachi. +Polankhulapo pa ganizoli, wapampando wa komiti yoyanganira za malimidwe mnyumba ya malamulo Joseph ChintantiMalunga adati ganizo la Admarc lofuna kugulitsa chimangacho ndi labwino polingalira kuti akufunika kubweza ngongole zomwe adatenga zogulira chimangacho. +Wachiwiri kwa mlembi wamkulu wa chipani cha Malawi Congress Elsenhower Mkaka adati ngati mpata ogulitsa chimangacho ungapezeke, Admarc igulitse koma ndondomeko yake iyende moyera. +Ndi ganizo lofunikira koma ziyende mwachilungamo komanso zisakwirire nkhani ya kagulidwe ka chimanga ku Zambia yomwe ikadali ikuyenera kuoneka mapeto ake, adatero Mkaka. +Pali malipoti akuti chaka chino anthu pafupifupi 1 miliyoni akhala ndi njala mdziko la Tanzania pomwe dziko la Kenya lawona ngamba yomwe silidawonepo kutanthauza kuti njala ivuta mdzikolo. +Malingana ndi mgwirizano wa maiko a mu Common Market for East and Central Africa (Comesa) maiko amayenera kugwirana manja wina a kapezeka ndi vuto ngati la njala. +Masiku apitawo, apolisi adagwira galimoto zomwe zimafuna kutulutsa chimanga kupititsa ku Tanzania kudzera mmaboma a Karonga ndi Chitipa. +Mneneri wapolisi James Kadadzera adati galimotozo ndi chimanga chomwe akuzisunga kudikira upangili wa boma kuti chimangacho atani nacho ndipo eni galimotozo adzazengedwa mlandu ofuna kuzembetsa chimanga. +Akuganizira mwana kupha bambo ake Kudalembedwa mBaibulo kuti masiku otsiriza mitundu idzaukirana ndipo ana nawo adzaukira makolo awo koma osati momwe zafikira Mponda T/A Nyoka mboma la Mchinji. +Mwana wina kumeneko akumusunga mchitokosi pomuganizira kuti adapha bambo ake pankhani ya malo. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mneneri wapolisi mbomalo, Moses Nyirenda, watsimikiza kuti apolisi akusunga Christopher Chirwa wa zaka 56 pomuganizira kuti adapha bambo ake Pataleo Chirwa wa zaka 90, powanyonga pakhosi malingana nzotsatira za kuchipatala. +Ndi mmene nkhani yonse ilili, tikukaikira mwana wa malemuyu pa zifukwa zingapo. Choyamba, adali limodzi tsiku lomwe malemuyo adakapezeka atafa. Chachiwiri, malemuyo adapezeka ali ndi chingwe mkhosi koma pamalo oti munthu sangadzimangilire ndipo chomaliza, achipatala adatsimikiza kuti malemuyo adafa kaamba kokhinyika, adatero Nyirenda. +Nthawi zambiri, anthu omwalira kaamba kodzimangilira, amapezeka akulendewera, kutanthauza kuti sikelo ya thupi lonse imathera pakhosi pomwe padina chingwe chodzimangiliriracho. +Chomwe chidazizwitsa anthu pa imfa ya bamboyu nchakuti adapezeka atakoledwa chingwe mkhosi ngati adadzimangirira koma thupi lonse lili pansi ngati wakhala tsonga ndipo nthambi yomwe idagwira chingweyo ili yowetezeka. +Patsikulo, lomwe ndi pa 16 July, 2016 mmawa, Nyirenda adati mwanayo adauza bambo ake kuti apite kudimbako akaunikirane za malire koma bamboyo sadabwerere mpaka pomwe adapezeka atafa mmunda wina wa mphepete mwa njira. +Nyirenda adati apolisi atafika pamalopo adatenga mtembo wa bamboyo nkupita nawo kuchipatala kuti akaupime pomwe mwanayo adapita naye kupolisi kuti afufuze nkhani yonse mwaufulu. +Kupewa kutsegula mmimba Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Nthenda ya kutsegula mmimba ndi imodzi mwa matenda omwe amakonda kufala kwambiri mnyengo ino ya mvula. +Malinga ndi dokotala wa pachipatala cha St Lukes mboma la zomba Siwale Shaime, kutsegula mmimba ndi pamene munthu akuchita chimbudzi cha madzi mopitirira kanayi pa tsiku. Iye adati, nthawi zambiri chomwe chimayambitsa matendawa ndi tizilombo tingonotingono tosaoneka ndi maso tomwe pa Chingerezi amatitchula kuti germs. +Zithaphwi zimasunga majelemusi otsegula mmimba Nyengo ino ya mvula, matendawa amachuluka chifukwa tizilomboti timakonda kupezeka pamalo a chinyontho ndipo timafala mosavuta ndi madzi komanso ntchetche, adatero dotoloyo. +Shaime adati mvula ikagwa, madzi othamanga amakokolola tizilomboti pamalo onyasa ndi kukatisiya mmisinje, mzitsime ndi malo ena okhala madzi. +Munthu akamwa kapena kugwiritsa ntchito madzi oterewa, tizilomboti timalowa mthupi mwake ndi kuyambitsa matendawa, adatero Shaime. +Iye adaonjezanso kuti ntchentche zimachuluka kwambiri nthawi ya mvula ndipo zimakatenga tizilomboti pamalo pomwe pali nyansi ndi kukaziika pa chakudya. +Ntchentche zikamva fungo la chinthu choola zimathamangira ndi kukatera pomwepo, pochoka zimanyamulapo tizilomboti ndi kukatiika pa chakudya ndipo wodya chakudyachi akhonza kutsegula nacho mmimba, adatero Shaime. +Iye adati ngakhale matendawa ndi oopsa, ndiopeweka ndipo ukhondo ndiye chida cha mphamvu. +Anthu akuyenera kusamba mmanja ndi sopo akangochoka kuchimbudzi, asanakhudze chakudya, akasintha mwana thewera, pofuna kuyamwitsa komanso kudyetsa mwana; kukhala ndi chimbudzi cha ukhondo pakhomo, kupewa kuchita chimbudzi paliponse, kusamala ndi kutaya zinyalala moyenera, kuvindikira chakudya, kutsuka zipatso asanadye, komanso kuteteza madzi akumwa pophitsa kapena kuthira mankhwala opha majeremusi, adatero dotoloyo. +Zili bwinoPAC Nduna yakale ya zaulimi George Chaponda yamangidwa patatha masiku 43 kuchokera pamene nthumwi kumsonkhano wa Public Affairs Committee (PAC) lidapatsa boma masiku 30 kuti limange ndi kuzenga mlandu ndunayo poyiganizira kuti idachita zachinyengo. +Imodzi mwa mfundo zimene nthumwizo zidamanga pamsonkhano umene udachitika mumzinda wa Blantyre pa 7 ndi 8 June, idali yoti Chaponda amangidwe malinga ndi kafukukufuku amene makomiti a Nyumba ya Malamulo adachita ndi kupeza kuti ndunayo idachita za chinyengo pogula chimanga ku Zambia. Komiti ina imene adakhazikitsa mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika idapezanso kuti Chaponda adachita ukapsala. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Chaponda (Kumanja) ndi Tayub kufika kukhoti Lachinayi Bungwe la ACB Lachitatu lidamanga Chaponda limodzi ndi mkulu wa kampani ya Transglobe Rashid Tayub komanso wapampando wa bungwe loona za malonda a mbewu zosiyanasiyana la Grain Traders Association of Malawi, Grace Mijiga Mhango. +Lachinayi, oyimira Chaponda adapempha bwalo la majisitileti kuti lichotse chikalata choti mkuluyo amangidwe koma bwalolo lidakana pempholo choncho adagonanso mchitokosi. Mhango adapatsidwa belo Lachitatu. +Ndipo madzulo a tsiku lomwelo, bwalolo lidapereka belo kwa Chaponda ndi Tayub. +Mneneri wa PAC Peter Mulomole adati akuyembekezera kuti ACB ipitiriza ntchito imene ayiyambayi mpaka kumapeto kuti chilungamo chidziwike. +Uku ndiko kukhala. Aliyense aziyesedwa ndi mlingo umodzi chifukwa palibe yemwe ali pamwamba pa malamulo. Chiyembekezo chathu tsopano nchoti momwe zateremu, ACB ikoka nkhaniyi mpaka kumapeto, adatero Mulomole. +Mkulu wa bungwe la Centre for the Development of People (Cedep), Gift Trapence, wati zomwe yachita ACB zaonetsa kuti bungweli layamba kugwira ntchito mosaopsezedwa. +Uku ndiye timati kukula. Bungwe la ACB siliyenera kugwira ntchito mwamantha kuopa maina. Apa tikuyembekezera kuti zonse ziyenda bwino mpaka chilungamo chioneke, adatero Trapence. +Mwezi wathawu, Chaponda adanena poyera kuti iye ndi wokonzeka kunjatidwa ngati Amalawi akuona kuti ndiwolakwa koma iye adabwereza kuti akudziwa kuti akufera kuthandiza Amalawi omwe akadafa ndi njala. +Aliza abale pa Khrisimasi chifukwa cha mowa Chaka chilichonse, 25 December ndi tsiku lachisangalalo koma chaka changopitachi lidali lachisoni mbanja la a Moses a kwa Chinthambwe mfumu yaikulu Chilowoko mboma la Ntchisi. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Patsikulo, mmodzi mwa a pabanjalo, Steven Moses wa zaka 47, adamwalira atamwa mkalabongo wochuluka komanso osadyera. +Mngono wa malemuyo yemwe amakhala kufupi naye ku Area 25 mumzinda wa Lilongwe, Amos Moses, adati mbale wakeyo adavomereza za nkhaniyo ndipo adati adamva kuchokera kwa wina kuti mbale wakeyo sanali bwino. +Amos: Idali imfa yowawa Iye adati mmbuyomo sadalandireko lipoti lilironse loti mbale wakeyo samamva bwino ndipo atamva uthengawo adathamangira kunyumba ya malemuyo komwe adakapeza atauma kale. +Tidamupeza atauma pamphepete pake pali mabotolo a mkalabongo, ena mulibe kanthu ena osayamba. Idali imfa yowawa, adatero Amos. +Mneneri wapolisi ya Kanengo, Alfred Chimthere, adatsimikiza kuti bamboyo adamwalira kaamba ka mowa. +Titalandira uthenga wa imfayo, tidathamangirako ndipo titatengera mtembowo kuchipatala cha Kamuzu Central, madotolo adatsimikiza kuti imfayo idachitika kaamba ka mowa oposa mlingo, adatero Chimthere. +Aaron Tsokwe, yemwe amagulitsa kanyenya mumsika wa Nsungwi komwe malemuyo amakonda kumwera mowa adati mkuluyu amakonda mowa wa kachasu ndi wa mmasacheti ndipo ngakhale amakonda mowa choncho, adalibe mbiri ya ndewu. +Anthu ambiri tidamuzolowera kuti amakhala chiledzerere. Iye kwake kudali kulongolola, osati ndewu, adatero Tsokwe. +Mkulu wa bungwe lolimbana ndi mchitidwe ogwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo la Drug Fight Malawi yemwenso amayendetsa mgwirizano wolimbikitsa kuti pakhale ndondomeko zoyendetsera kagwiritsidwe ntchito ka mankhwala wa Malawi Alcohol Policy Alliance, Nelson Zakeyu, adati imfa zotere zikunka patsogolo kaamba kosowa ndondomeko zoyenera. +Iye adati izi zikadatha boma likadakhala ndi ndondomeko zoyenera komanso njira zamphamvu zoonetsetsa kuti ndondomekozo zikugwiradi ntchito. +Timatsogoza kunena kuti anthu azidyera akafuna kumwa mowa mmalo mongoletsa kuti anthuwo asamamwe, adatero Zakeyu. +Mneneri wa polisi mdziko muno James Kadadzera adauza Msangulutso Lachinayi kuti ali mkati mosonkhanitsa ngozi zomwe zachitika mkatikati mwa nyengo ya zisangalalo ntchito yomwe ikukhudza kusonkhanitsa chiwerengero cha imfa zokhala ngati ya Steven. +Iye adati apolisi amagwira ntchito usana ndi usiku kuwonetsetsa kuti anthu akutsatira malamulo ndi cholinga chopewa zinthu zosakhala bwino monga imfa zopeweka ngati za uchidakwa. +Malamulotu alipo monga pamlingo wa zaka zovomerezeka kumwa mowa, nthawi yomwera mowa komanso mamwedwe oyenera. Ichi nchifukwa chake nthawi zina apolisi amayendera malo omwera kufuna kuona ngati ndondomeko zikutsatidwa, adatero Kadadzera. +Fodya wobwerera kumsika amugulitsa Mkulu wa bungwe la Tobacco Association of Malawi (Tama), Graham Kunimba, wati fodya yemwe anabwerera pamsika chaka chino tsopano amugulitsa. +Iye adati ngakhale zinthu zinavuta, bungwelo lidayesetsa kukambirana ndi boma, bungwe la Tobacco Control Commission (TCC) ndi ogula kufikira tsopano fodya yense amugulitsa. Mwa magawo 100 alionse a fodya wofika kumsika, 70 akhala akubwezedwa chaka chino, ndipo alimi ambiri manja anali mkhosi kusowa chochita naye. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Alimi a fodya ngati uyu ayenera kukhala ndi zitupa Kunimba wati malonda a fodya mchakachi anavuta kwambiri chifukwa fodya analimidwa wochuluka kwambiri kuposa mlingo omwe ogula amafuna. Kafukufuku akusonyeza kuti dziko la Malawi limayenera kulima fodya okwana makilogalamu 158.1 miliyoni koma chaka chino tinakolola makilogalamu 205.53 miliyoni. +Ngakhale fodyayu amugula, mitengo yake inali yotsika kwambiri. Izi zapangitsa kuti dziko lino lipeze ndalama zochepa ku ulimiwu kusiyana ndi chaka chatha. Kafukufuku akusonyeza kuti chaka chatha dziko la Malawi lidapeza K216.8 biliyoni kuchokera ku fodya, koma chaka chino tapeza K162.6 biliyoni. +Pamenepa ndiye kuti boma lapeza ndalama zochepa komanso msonkho wochokera ku ulimiwu wachepa ndipo mwachidziwikire chuma cha boma chakhunzidwa, adatero Kunimba. +Mkulu wa bungwe la Farmers Union of Malawi (FUM), Alfred Kapichira-Banda, wavomereza za kugulitsidwa kwa fodyayu ndipo adati fodyayu amugula mongolanda. Fodya wambiri amugula pamtengo wa K553 pa kilogalamu ndipo wina amugula kuchepera apo, adatero Kapichira-Banda. +Mmodzi mwa alimi omwe anakhudzidwa ndi vutoli, Isack Banda wa mboma la Dowa, wati zomwe wakumana nazo mchakachi zayamba kumupatsa maganizo osiya ulimiwu chifukwa sanapeze phindu lililonse. +Ulimi wa fodya umalowa zambiri komanso umalira zipangizo zochuluka ndi zokwera mtengo moti ndikawerengetsa zonsezi palibe chimene ndaphula koposa ndingoleka, adatero Banda. +Bungwe la Tama likuchenjeza kuti mlimi amene sanalandire chilolezo kuchokera ku TCC asalime fodya chifukwa sadzagulidwa kumsika. +Bungweli lati izi zithandiza kuti fodya yemwe alimidwe chaka chino asapyole mlingo omwe dziko la Malawi likuyenera kulima. Kunimba adati alimi omwe alandira chilolezochi apatsidwa mlingo wa fodya yemwe akuyenera kulima. +Tikuwalangiza alimi onse kuti asatire mlingo omwe TCC yawapatsa ndipo asapyole, kuopa kuchulutsa zokolola zomwe zingapangitse kuti malonda adzavutenso chaka chamawachi, adatero Kunimba. +Agwira othandiza akunja kupeza zitupa zaunzika Mmiyezi iwiri yokha chiyambireni kalembera wa zitupa za unzika, Amalawi ena ayamba kugwidwa akuthandiza nzika za mayiko ena kupeza zitupazi. +Akuluakulu ena ati uku nkusowa chikondi ndi dziko lawo la Malawi. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ntchito ya kalembera ili mkati mchigawo cha pakati Nzika zitatu za ku Mozambique zagwidwa kale mboma la Dedza pomwe zimafuna kulembetsa mkaundulayu pamalo olembetsera a Umbwi mothandizidwa ndi mayi wa Chimalawi. +Mneneri wapolisi ku Dedza Edward Kabango adati nzika za ku Mozambique ndi Samalani Joseph wa zaka 21, Patrick Machaka wa zaka 32, Chewami Ali wa zaka 25 ndipo onse ndi ochokera ku Angonia, mchigawo cha Tete ku Mozambique pomwe mzimayiyo ndi Angellina Lameck wa zaka 36 wochokera mmudzi mwa kapalamula ku Dedza. Iwo akaonekera kukhoti posachedwa. +Mneneri wa nthambi yoyendetsa kalemberayu ya National Registration Bureau (NRB) Norman Fulatira watsimikiza kuti mzimayi wa ku Malawi wamangidwa limodzi ndi nzika za ku Mozambique pomuganizira kuti amafuna kuzithandiza kupeza zitupa za unzika. +Iye adati mayiyo akumuganizira mlandu wofuna kuthandiza nzika za dziko lino kupeza zitupa zaunzika popereka umboni wabodza, motsutsana ndi malamulo a pulogalamuyi. +Boma likufuna kuthandiza Amalawi popangitsa zitupazi chifukwa nzika za maiko ena zakhala zikuwadyera masuku pamutu ndiye Amalawi omwewo akuthandizanso alendowo kupanga chinyengo, kumeneku nkusowa umunthu, watero Fulatira. +Iye wati kuthandiza nzika za mayiko ena kulembetsa mwachinyengo ndi mlandu pa malamulo a nthambiyo ndipo munthu akhoza kukasewenza zaka 5 ndi kupereka chindapusa cha K1 miliyoni akapezeka wolakwa. +Kabango wati awiri mwa anthuwo adapezeka ndi zitupa za unzika za mdziko la Mozambique ndipo adavomera kuti amafunadi kupeza zitupa za unzika wa Malawi. +Titawafusa bwinobwino adaulula kuti cholinga chawo chidali choti azitha kulandira thandizo la zaumoyo mzipatala za ku Malawi mosavuta. Akuti kwa iwo, thandizo la msanga la za umoyo amalipeza ku Malawi, adatero Kabango. +Iye adati anthuwa akuimbidwa mlandu wopereka umboni wabodza kwa akuluakulu a kalembera zomwe zikutsutsana ndi gawo 43 la malamulo oyendetsera ntchito za NRB. +Pochita kalemberayu, nthambiyo ikufuna umboni ochokera kwa mafumu kapena zitupa zina monga zoyendera, zoyendetsera galimoto, zakubadwa kapena ukwati, zomwe zikusonyeza kuti munthu ndi Mmalawi. +Apa zikutanthauza kuti wofuna kuthandiza alendo kupeza zitupa za unzika, awathandize kupeza umboni onsewu, zomwe zikutanthauzanso kuti mkatikati mwa dongosololo mwadutsa katangale omwe ndi mlandu wina pa malamulo a dziko lino. +Mneneri wapolisi, James Kadadzera, wati mchitidwewu ndi wobwezeretsa zinthu mmbuyo chifukwa njira ya zitupayi ndi imodzi mwa njira zomwe boma likufuna kuti lizidziwira nzika zake kupangira pa mavuto komanso kowopetsa nzika za mayiko ena kupanga zaupandu mmawanga Amalawi. +Zitupazi zikulowa pambiri chifukwa kuchitetezo nako zikukhudzako. Mmbuyomu tidali ndi vuto loti nzika za mmaiko ena zimatha kupanga chiwembu nkumaoneka ngati Amalawi ndiye zimayipitsa mbiri yathu. +Ntchito ya zitupayi ikayenda bwinobwino ndiye kuti mavuto onsewa adzatha chifukwa tizidziwana kuti uyu ndi Mmalawi kapena ongobwera kotero chitetezo chikhwima komanso mbiri yathu siyionongeka, watero kadadzera. +Nduna ya za mdziko ndi chitetezo Grace Obama Chiumia wati Amalawi akuyenera kukhala ndi mtima wokonda dziko lawo pothandiza boma kukwaniritsa ndondomeko zomwe cholinga chake nkuwatumikira mwaukadaulo. +Pologalamu ya zitupa si ya munthu kapena mtundu ayi koma ya Amalawi ndiye tikuyenera kugwirana manja tonse nkuthandizana ndi boma kuti pologalamuyi iyende bwino chifukwa patsogolo ndife tomwe tidzaimve kukoma, watero iye. +Gwamba wochokera kubanja loimba Mdziko muno muli oimba osiyanasiyana. koma kukamba za oimba nyimbo zauzimu, Gwamba ndi mmodzi mwa oimba amene akusintha miyoyo ya anthu pa Malawi pano. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere: Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Gwamba: Ndi nyimbo zokoma kwambiri Gwamba, ndimasule kuti ndikudziwe bwinobwino mmachezawa. +Dzina langa lonse ndi Duncan Gwamba Zgambo omaliza mbanja la ana anayi ndipo kwathu ndi mboma la Rumphi ku mpoto kwa dziko la Malawi. +Anthu ambiri amangoti Gwamba, tawauze kuti kodi Gwambayo ndi wotani ndipo amakonda chiyani. +Zikomo kwambiri, Gwamba ndi dzina lomwe ndimatchukadi nalo ngati oyimba koma munthune ndimapanga zambiri monga mabizinesi ndi zina. Kuimbaku ndi chimodzi mwa zochita zomwe ndimapanga pamphepete pa mabizinesi. +Kodi iweyo zoimbazi udayamba bwanji? Funso labwino ndipo anthu ambiri amandifunsa zimenezi moti ndikayankha iweyo ndiye kuti ndayankha anthu ambiri nthawi imodzi. Munthune ndimachokera ku banja la zoimbaimba. Malume anga, Bright Nkhata, adali munthu waluso kwambiri pa zoimba moti ambiri amamudziwa bwino. Kupatula apo, malume anga ena, Bernard Kwilimbe, nawonso ndiwokonda zoimba kwambiri moti oimba ena mMalawi muno adaphunzira kwa anthu awiri amenewa. Mwachidule, zoyimbazi ndi za mmagazi osati kuchita kuphunzira kapena kukakamiza ayi. +Watulutsa chimbale posachedwapa, kodi udachitulutsa liti ndipo chimatchedwanji? Chimbale chimenechi chikutchedwa Jesus is my Boss kutanthauza kuti Ambuye Yesu ndi bwana wanga. Ndi nyimbo ya uzimu yokoma kwambiri ndipo ili ndi tanthauzo ndi chiphunzitso chapamwamba kwa okhulupilira. +Chimbale chimenechi chidakhazikitsidwa pa 24 December 2016 ku Bingu International Convention Centre (BICC) ija ena amati 5 Star Hotel. +Chimbalechi chili ndi nyimbo zingati ndipo zina mwa izo ndi ziti? Chimbalechi chili ndi nyimbo 11 ndipo papita luso ndikudzipereka kuti chituluke ndi kumveka momwe chimamvekeramu. Kudatengera kudzipereka kwa anthu angapo monga oimba, ojambula ndi azipangizo omwe. Muli nyimbo monga Anabwera Yesu yomwe ndimayikonda kwambiri komanso ndiyo yoyambirira. Mulinso nyimbo yotchedwa Bwana yomwe adathandizira Lulu ndipo nayonso ndi nyimbo yokoma kwambiri. Mwachidule, nyimbo zomwe zili mchimbalechi nzokoma zokhazokha. +Akufuna chakudya ku Nsanje Ngakhale maboma ambiri zikuoneka kuti apata chakudya mnyengo ya ulimi yangothayi, anthu ena mboma la Nsanje ati akufuna thandizo la chakudya lomwe mabungwe ndi boma amapereka lipitirire kwa miyezi ina itatu chifukwa sanakolole chimanga chokwanira ndipo ali pa njala. +Phungu wa dera la kummwera kwa bomali, Thomson Kamangira, adanena izi pamsonkhano wa chitukuko omwe nduna yofalitsa nkhani Nicholas Dausi idachititsa podziwitsa anthu pulojekiti ya boma yoonetsetsa kuti netiweki ya lamya ikupezeka mmaboma onse mosavuta yotchedwa Malawi National Fibre Backbone sabata yatha. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Dausi: Tiyesetsa anthu asafe Kamangira adati ngamba yomwe inagwa chimanga chitangomasula ngayaye inasokoneza mbewu mbomalo. +Tikusowa zambiri koma pakali pano vuto ndi la njala. Izi ndi kaamba ka ngamba osati madzi osefukira. Mabungwe asiya kupereka chakudya, koma tikuwapempha kupitiririza kwa miyezi itatu kuti tipulumuke ku njala yomwe itisause posachedwapa, adatero Kamangira. +Pothirira ndemanga, khansala Robert Chabvi adati anthu mderalo chaka chinonso zawavuta kumunda ndipo boma ndi mabungwe awapase zida zochitira ulimi wamthirira. +Sikuti ndife opemphetsa koma chimanga chatilakanso chaka chino. Boma ndi mabungwe tipatseni zida za ulimi wamthirira zoyendera mphamvu ya dzuwa kuti tilimenso uku mukutipatsa thandizo la chakudya. Pokhala kumudzi, anthu alibe chuma chogulira chimanga kwa mavenda kapena ku Admarc, adatero Chabvi. +Poyankhapo, Dausi adati anthu asadere nkhawa chifukwa mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika achita zotheka kuti aliyense asafe ndi njala. +Izi zikusemphana ndi lipoti la boma la mu February lomwe linati chimanga chikololedwa chochuluka matani 3.2 miliyoni kusiyana ndi chaka chatha 2.3 miliyoni. +Malinga ndi mkulu wa Farmers Union of Malawi (FUM) Alfred Kapichira Banda nzosadabwitsa kuti anthu ena ku Nsanje adandaule za njala. +Zolosera pa zokolola sizimasonyeza momwe zinthu zilili, adatero iye. +Chipembedzo chikukolezera kupemphapempha mmisewu Kukhulupirira chipembedzo kukukolezera mchitidwe wopemphapempha mmisewu, zimene zachititsa kuti ntchito yochotsa opemphawa ivute, watero mkulu wa bungwe limene limachotsa ana mmisewu la Chisomo Childrens Club. +Ngakhale boma lakhala likulengeza kuti aliyense wopezeka akupemphetsa mmisewu adzamangidwa, izi sizikutheka. Sabata zingapo zapitazo, bomalo limalengeza mozungulira mzinda wa Blantyre kuti aliyense wopezeka akupereka ndalama kwa opemphetsa adzamangidwa. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Akuti mawu a Mulungu amavomereza kupereka kwa opempha Koma mkulu wa bungweli Auspicious Ndamuwa wati ganizo lochotsa opemphetsa mmisewu silingakwaniritsidwe chifukwa zipembedzo zambiri zimalimbikitsa kupereka. Iye adati chikhulupiriro chopereka chidayala nthenje pakati pa Akhristu ndi Asilamu. +Opemphetsawo amadziwa kuti akapita mmisewu, akakumana ndi anthu opemphera ndiponso a chisoni omwe akawapatse ndalama. Ana ena tikawatenga timawapatsa zofunikira pamoyo wawo, koma ena okonda ndalama ndi kudana ndi sukulu amathawa nkubwerera mmisewu. Akanakhala kuti anthu sapereka ndalama, vutoli bwenzi litatha, adatero Ndamuwa. +Akhristu akuganiziridwa kukolezera mchitidwewu pofuna kukwaniritsa mawu a pa Machitidwe a Atumwi 20:35 omwe akuti: Mzinthu zonse ndakuonetsani kuti mwakugwira ntchito molimbika chomwechi, muthandize ofookawo, ndipo muzikumbukira mawu a Ambuye Yesu. Pajatu iye anati, Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira. +Ndamuwa adati Asilamu akutichita izi chifukwa cha Zakati yomwe ndi imodzi mwa ngodya za chipembedzo chawo yomwe achuma amatenga phindu lomwe apeza ndi kugawirako osowa. +Koma mlembi wa Blantyre City Presbytery yomwe ndi gawo la Sinodi ya Blantyre mbusa Baxton Maulidi adati mpingo umathandiza osowa osati kulimbikitsa mchitidwewu chifukwa nthawi ya Yesu opemphetsa adaliponso. +Iye adati vuto ndi kusathandiza anthuwa mokwanira powapatsa njira zoyenera za kapezedwe ka chuma. +Kulumala, ulesi ndi umphawi zimachititsa anthu kupita pamsewu. Koma palinso olumala ochuluka omwe akugwira ntchito ndi kumathandiza alungalunga. +Akhristu sangasiye kuthandiza ena. Chofunika ndi kupeza njira zokhazikika zoti azidalira osati kupempha. Munthu wopemphetsa yemwe Petulo mBaibulo adamuchiritsa sadabwerere pamsewu chifukwa adamuthandiza moyenera, adatero Maulidi. +Ndipo Sheik Alli Makalani wa pa mzikiti wa pa Mangochi pa boma adati Zakati siyikukhudzana ndi anthu opemphetsa chifukwa Chisilamu chimalimbikitsa kugwira ntchito komanso kholo kusamalira ana ake. +Wololedwa kupempha ndi mwana wamasiye yemwe alibe womuthandiza ndi wolumala woti sangagwire ntchito. Koma thandizo lake siliyenera kupempha kumsewu. Amatengedwa ndi kukasamalilidwa kumalo oyenera. Sitikondwera ndi opemphetsa mwadala, iye adatero. +Maulidi ndi Makalani adapempha mabungwe, azipembedzo ndi boma kuti apeze njira zokhazikika zothandiza osowa. +Mneneri wa nthambi ya zosamalira anthu Lucy Bandazi adagwirizana ndi pempholo, koma adati ambiri kupemphetsa ndi khalidwe chabe chifukwa adapindula mundondomeko za boma zowathandiza kuima paokha. +Pali njira ya mthandizi, feteleza wotsika mtengo ndi zina mmatumba a chitukuko. Undunawu umapereka ukadaulo wa ntchito za manja kwa omwe ali ndi ulumali kudzera ku Malawi Council for the Handicapped (Macoha) ndi Mulanje School for the Blind komwe amaphunzira kusoka, kuluka, ukalipentala ndi ulimi. Akamaliza amapatsidwa zipangizo zoyambira moti ambiri akupemphetsa mmisewu adapindula mu ndondomekozi, iye adatero. +Bandazi adati aliyense opereka ndalama kwa opemphetsawa akuthandizira kuphwanya lamulo. +Mavuto omwe amawapititsa mmisewu sangathe ndi kupemphetsa. Ndondomeko za boma ndi zofuna kuti apeze zochita zokhazikika zomwe zipaso zake sizingaoneke nthawi yochepa. Ndi udindo wa aliyense kuonetsetsa kuti anthu osowa akukhala umoyo wabwino, osati mmsewu, adatero Bandazi. +Anatchezera ANATCHEREZA Akundikakamira Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndili ndi mkazi yemwe ndili naye mwana mmodzi. Vuto lake ndi limodzi: amakhalira kunyoza makolo ndi abale anga. Amati banja sakulifuna koma ndikati amange zake, amakakamira. Ndichitenji? H, Blantyre. +Zikomo H, Kodi banja lanu mudamangitsa kuti? Kodi mudangogwiriziza kwa ankhoswe? Ngati ndi choncho bwanji osakatula nkhawazo kumeneko? Ngati mudamangitsa kumpingo, mukhonzanso kupita uko akakuthandizeni. +Banjatu sakakamiza ndipo apapa zikuonetseratu kuti mkazi wanuyo ali ndi chibwana komanso musakaike, ameneyo ali ndi wina amene amamulimbitsa mtima. Nkutheka kuti winayonso ali pabanja ndipo amamunamiza kuti adzasiya mkazi wake ndi kutengana ndi wanuyo. +Izi si nkhambakamwa, ndipo mumufufuze bwino mayendedwe ake. Samalani naye mudzalirira kuutsi atakubweretserani kwayauotche. +Akuti ndidzamukwatire iyeyo basi Zikomo agogo, Bambo ndi mayi anga adasiyana ukwati ndipo adakwatirana ndi mkazi wina yemwe analinso ndi ana ena. Mmodzi mwa anawo ndi wamkazi ndipo ndamulera mpaka kusukulu ya ukachenjede kumene akuphunzira panopa. +Vuto langa nali, iyeyo akuti sakufuna adzamve zoti ndakwatira mkazi wina chifukwa amandikonda kwambiri. Iye adati adzamuikira chiphe mkazi amene ndingadzakwatire. +Iyeyo akuti ndi bunthu ndipo akuti sadzalola mwamuna aliyense kudzamuyamba koma ine ndekha. Iyeyotu amati palibe chibale pakati pa ine ndi iyeyo. Ndichitenji? TD, Lilongwe. +TD Monga ndanena, banja sakakamiza. Chikondi chili ngati fupa, ukakakamiza, mphika umasweka. Apatu mlongo wanuyo ayenera kuti palibe angakakamize wina kukonda mnzake, mapeto ake ndi ngozi. +Chomwe muyenera kumuuza nchakuti, si kuti munthu akakuchitira zabwino ndiye kuti nawenso udzikakamize kubwezera zabwino, kuphatikiza zimene zili zosadziwika bwino. Tamvapo za amayi ena amene apatsidwa mimba komanso matenda ndi abambo ena amene amawathokoza powapatsa ntchito. +Mumuuzitse kuti pamene mumamuthandiza, si kuti mumayembekezera kuti adzabwenza china chake. +Tionana 2019 Mafumu Mafumu achenjeza kuti aphungu omwe sakufuna kumva madandaulo awo pankhani ya lamulo lokhudza malo a makolo adzakumana ndi chipande pachisankho cha 2019. +Izi zidanendwa Lachitatu pomwe mafumu ochokera mbali zosiyanasiyana motsagana ndi womenyerera ufulu wa anthu pankhani malo mmaboma a Thyolo ndi Mulanje, Vincent Wandale, adakapereka chikalata cha madandaulo awo ku Nyumba ya Malamulo. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mafumu kuchokera zigawo zonse mdziko muno patsiku la chionetsero Nkhani yomwe mafumuwa ikuwapweteka ndi yosintha lamulo lokhudza malo a makolo omwe iwo akuti amayenera kukhala pansi pa ulamuliro wawo pomwe lamulo latsopanoli likuti anthu azikhala ndi ulamuliro pamalo otere. +Lamuloli lidasinthidwa mNyumba ya Malamulo ndi kuvomerezedwa ndi mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika mwezi wa September chaka chino, koma mafumuwa akufuna kusinthaku kubwezedwe mpaka iwo adzafunsidwe maganizo awo pankhaniyi. +Gululi, lomwe lidakumana ndi mavuto kuti lipereke madandaulowo ku Nyumbayi, lidanyamula zikwangwani zochenjeza kuti aphungu omwe adasintha lamuloli adzawafuna mu 2019 chisankho chikafika. +Mafumu kuchokera zigawo zonse mdziko muno patsiku la chionetsero Zikwangwani zina zidati: Akuluakulu a zamalo yeserani kubwera mmadera mwathu mudzaone chidameta nkhanga mpala komanso, A Pulezidenti ndi aphungu ikani maso anu pa 2019. +Mudandaulo lawo mchikalata chomwe adapereka kwa aphungu ndipo adalandira ndi mtsogoleri wa mbali yotsutsa boma yemwenso ndi pulezidenti wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP), Lazarus Chakwera, mafumu adati malo a makolo ndi awo osiyiridwa ndi makolo. +Pothirirapo ndemanga, Wandale, yemwe akuyimirira anthu a ku Thyolo ndi Mulanje, adachenjeza boma kuti lisiye kupondereza anthu chifukwa cha malo awo omwe. +Atalandira chikalata cha madandaulocho, Chakwera adatsimikizira mafumu ndi gululo kuti madandaulo awo akafika mNyumba ya Malamulo kuti akaunikidwe. +Koma ndunda ya zamalo ndi chitukuko cha mmidzi, Atupele Muluzi, akutsindika kuti lamulo latsopanoli ndi lopindulira anthu akumudzi powapatsa mphamvu zolamulira malo omwe akugwiritsa ntchito. +Lamulo lakale limatanthauza kuti malo a makolo ndi a gulu, choncho munthu sangamasuke kupanga nawo chitukuko chenicheni. Chomwe lamulo latsopanoli likubweretsa nchakuti munthu azikhala ndi makalata osonyeza umwini moti akhoza kukatengera ngakhale ngongole ku banki ngati chikole chifukwa pali umboni kuti ndi malo ake, adatero Muluzi. +Iye adati lamuloli likuperekanso mpata kwa achinyamata ndi amayi okhala ndi malo mdzina lawo kutanthauza kuti amayi ndi ana amasiye azikhala otetezedwa kunkhanza zolandidwa malo. +Tipulumutseni ku ukwati wa ana Amati ana ndi tsogolo la mawa. Koma zikuchitika ku Neno zikukaikitsa ngati adzakhaledi atsogoleri mawa. +Kumeneko ukwati wa ana akuti wafika pa lekaleka ndipo ngati boma ndi mabungwe sachitapo kanthu, zinthu zifika poipitsitsa. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Lachinayi sabata yatha bungwe la Save the Children lidaitanitsa Nyumba ya Malamulo ya ana komwe anawa adatula nkhawa zawo kwa atsogoleri. Nyumbayo idakumana masiku awiriLachinayi mpaka Lachisanu. +Momwe zimachitikira sizimasiyana ndi momwe imakhalira Nyumba ya Malamulo ya dziko lino chifukwa mudali sipikala komanso aphungu. +Zonsezi zimachitika ndi ana amboma la Neno amene amachokera msukulu zosiyanasiyana za mbomalo. +Malinga ndi mlangizi wa ana ku bungweli, Thandizolathu Kadzamira, anawa adachita kusankhana kuti apeze owayimira pa sukulu yawo. +Amasankha phungu wawo amene akawalankhulire mnyumbayi ikamakumana. Adasankhanso sipikala wawo. Awatu ndi masukulu ambiri a mboma lino, adatero Kadzamira. +Mnyumbayi, anawa adalankhula Chingerezi ndi Chichewa osachita mantha ngakhale holo ya Neno idakhoma ndi anthu ofuna kudzaonera nkhumanoyo. +Nkhani zidamanga nthenje mnyumbayi zidali zodandaulira boma komanso mabungwe kuti awapulumutse ku maukwati a ana omwe akolera mbomalo. +Anawa adapemphanso kuti boma liwamangire sukulu zabwino ndi kuikamo zipangizo zoyenera. +Sipikala wa nyumbayo, Trifonia Kaduya, wa zaka 14 ndipo akukalowa folomu 2 pa sekondale ya Chiwale, adati akuluakulu asiye kuimba nyimbo ndipo ayambe kuchita. +Timalankhula koma palibe chimachitika. Nkhumano ino tikufuna akuluakulu athu ayambe kuchita, adatero. +Mwana wa zaka 14 umupeza wakwatiwa kale. Kodi apa palinso lonjezo loti mawa tidzakhala atsogoleri? adadabwa sipikalayu. +Wotsogolera komiti yokhudza ana ku Nyumba ya Malamulo, Richard Chimwendo Banda, adalonjeza sipikala Kaduya kuti nkhawa zawo ziyankhidwa. +Alankhula mopanda mantha. Izi ndi zomwe tikufuna kuti zithandizire chidwi chathu chofuna kuthandiza ana. Amve kwa ine kuti tichitapo kanthu, adatero Banda. +Iye adati Nyumba ya Malamulo ya dziko lino ikamakumana adzatenga ena mwa anawa kuti akalankhule kunyumbayi cholinga aphungu akadzimvere mavuto amene anawa akukumana nawo. +Kuikira kumbuyo khalidwe loipa Zimanenedwanenedwa zinthu ngati izi kwa amayi okwatiwa: Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Osamasiyira Anaphiri kuti azingophikira abambo, kenaka akulandani banja Osaleka kudzisamalira chifukwa bamboyo maso alunjika pena Pakhomo kumasamalira chifukwa uve umathamangitsa bambo Izi ndi zitsanzo chabe, koma pali zambiri zomwe mzimayi amachenjezedwa kuti asamalitse pofuna kusunga banja. +Tikaonetsetsa palibe vuto ndi kusamala pakhomo, kudzisamalira ndi zina zotero, koma nzolakwika kuika zinthuzi ngati zida zothandizira kuti bambo akhazikike pakhomo. +Chifukwa polankhula moterendipo izi zimalankhulidwa kwambiri mmalo achilangozotimakhala ngati tikuvomereza kuti zina mwa izi ndi zifukwa zoyenerera popangitsa kuti bambo azinka nachita zibwenzi chifukwa mkazi wake walephera penapake kunyumba. +Kunena zoona abambo ena amakhala ndi zofooka zina zikuluzikulu zomwe amayi amazipirira mmakomomu osaganizirakonso kuti mwina apeze mpumulo popeza chibwenzi. +Nchifukwa chiyani zimaoneka zabwinobwino kuti abambo azilephera kupirira nkhani ngati za chakudya nkufika pomasirira Naphiri kuti mpaka apange naye chibwenzi chifukwa waphika bwino? Abambo otere ngachimasomaso ndipo amakhala kuti Naphiriyo amamusirira kale. Ndiye malankhulidwe omamuuza mkazi kuti akulekerera amakhala akuikira kumbuyo makhalidwe onyansa. +Pali abambo ena autchisi, ena oti akavula nsapato fungo nyumba yonse. Sudzamupeza mayi akuti bola Joni okonza maluwa amadzisamalirako. Mmalo mwake mayi amayesetsa kuti akonze nsapato ndi sokosi za mwamuna wake kuti fungo lichepe. +Koma mzimayi akamveka thukuta, ndiye bambo ali ndi chifukwa chomveka bwino choti akasake chibwenzi? Osamuuza mkazi wako za vuto lake nkuthandizana naye kupeza njira zothetsera fungo la thukutalo bwa? Mundimvetse, sindikuti amayi atayirire, koma tizindikire kuti amayi amakhala ndi zofooka. Tsono zofooka za amayi zisakhale zifukwa zokwanira zoti abambo azinka nasaka akazi ena. +Idali nthawi ya mapemphero Mtsikana akadzakulembera SMS yoti I care for you ndiye kuti zatheka chifukwa uthengawu ndi waukulu kwambiri. Zidayambanso choncho ndi Alison Banda wa Dziko FM yemwe akukaveka mphete Chifundo Namale pa 30 July 2016. +Awiriwatu akuti akhala akukumana nthawi ya mapemphero ku Calvary Family Church ku Falls mumzinda wa Lilongwe. Inde ndi nthawi ya mapemphero komabe Alison amaponya maso moti pa 30 July kuli kanthu ku Area 36 kulikulu la dziko lino. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Alison ndi Chikondi amangitsa woyera ku Lilongwe Mapemphero ali apo, Alison akuti mmutu mwake mudabwera mawu achikondi kuti akuyenera aponye pa namwaliyu. Zidatheka koma adamukana. +Mphini yobwereza ndiyo imawala, adabweranso ndi nzeru zina koma namwaliyo adapukusabe mutu kukanitsitsa kuti sakufuna zachibwana. +Mkazi adavuta kuti alole, amaona ngati poti ndine wotchuka sindili siliyasi, adatero Alison wa mmudzi mwa Kapindula kwa T/A Kaomba mboma la Kasungu. +Ndidayata chikhulupiriro. Kenaka kudabwa wanditumizira uthenga ati wandisowa. Ine chiyani? Kenakanso watumiza uthenga wina ati I care for you. Ndidadziwiratu kuti basi ndawina mtima wake, adatero. +Mosachedwa, akuti adapanga kaulendo kuti akumane ndi namwaliyu, yemwe ndi wa mmudzi mwa Gonjo kwa T/A Mthiramanja mboma la Mulanje, ndipo pa 19 February adakumana ndi namwaliyu kuseli kwa NBS Bank mumzindawo ndipo chibwenzi chidayamba. +Chifundo amene ndi mphunzitsi kukoleji ya Exploits University akuti adalola Alison chifukwa cha khalidwe lake. +Ndinene chiyani ine? Alison ndi munthu wolemekezeka, wokonda, wansangala, ndipo pali zambiri zomwe ndinganene zokhudza mnyamatayu. Pamene ndimati ndimudziwe kaye ndi pamenenso ndimagwera mchikondi, komanso amakonda Mulungu, adatero Chifundo. +Chipatala cha boma chitsekedwa loweruka Miyoyo ya anthu pafupifupi 50 000 ozungulira chipatala cha Mkanda Health Centre mboma la Mchinji imaikidwa pachiopsezo Loweruka chifukwa sichitsekulidwa patsikulo mosemphana ndi dongosolo la unduna wa zaumoyo. +Mneneri wa unduna wa zaumoyo Adrian Chikumbe adauza Msangulutso Lolemba kuti chipatalacho chimayenera kutsekulidwa ndi Loweruka lomwekuchoka mmawa mpaka nthawi ya nkhomaliro. Kuposera apo, madotolo amayenera kusamala odwalika zedi kapena a matenda obwera mwadzidzidzi. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ngakhale izi zili choncho, chipatalachi chimalandiranso odwala kuchokera mzipatala zina zazingonozingono 5, omwe akafika pamalopa Pachiweru, amakhala kakasi. +Kafukufuku wathu wasonyeza kuti chipatalachi sichimatsekulidwa Loweruka chifukwa mkulu woyanganira pamalopa, yemwe sitimutchula dzina, amapemphera tsikulo. +Ndipo kusatsekulidwa kwa chipatalachi kukuchititsa ena mwa anthu ofuna thandizo kupita kuzipatala zomwe si zaboma kapenanso chipatala cha Tamanda chomwe chili mdziko la Zambia. +Bambo wina, yemwe adakana kutchulidwa dzina, adati mwana wake wa zaka 12 amene adafika naye pachipatalapo kumapeto kwa 2015 adamwalira kaamba kosowa chisamaliro. Iye adati adapita ndi mwanayo akuonetsa zizindikiro za malungo Lachisanu nthawi itadutsa 11 koloko usiku koma dotolo adakana kuwathandiza usikuwo. +Adakana kudzuka ndipo patadutsa maola awiri mwanayo adamwalira. Apa tidapempha mlonda kuti akawauze kuti mwanayo watisiya ndipo atithandize koma adangomuuza kuti tizipita kumudzi, adatero bamboyo, Wina mwa okhudzidwa ndi vutoli, yemwe ndi mphunzitsi pa sukulu ya sekondale mderalo, adati wabwererapo kawiri konse mchaka chathachi pachipatalachi. +Ulendo wina, mwezi wa October, ndidabwerera ndi mwana wanga wa zaka zitatu yemwe amadwala mphumu. Chifuwachi chitakwera cha mma 7 koloko usiku wa Loweruka, ndidathamangira kuchipatala komwe ndidapezako anthu ena awiri odwala akudikirira, adatero iye. +Iye adaonjeza kuti atabwera mkulu wa pachipatalapo, adawanyengerera kuti awathandize ndipo adangowalembera enawo kuti azipita chipatala cha kuboma. +Koma mwana wanga adakanitsitsa kumulemba mpaka adatibweza, adatero munthuyo yemwe wakana kutchulidwa dzina. +Iye adapita kuchipatala cholipira komwe adalipira K4 500. +Mkulu wa komiti ya kayendetsedwe ka chipatalacho ya health advisory committee (HAC) Thomas Bisiketi adatsimikiza kuti odwala saonedwa patsikulo ndipo mbali ya amayi obereka yokha ndi yomwe imakhala ikugwira ntchito. +Mkulu wachipatalapo sagwira ntchito patsikuli, koma ife ngati a HAC timaoona ngati ndi momwe zipatala zonse zaboma satsegula Loweruka, adatero Bisiketi. +Malinga ndi wapampando wa komiti ya chitukuko kwa mderali Anorld Chitedze, chipatalachi chakhala chisakutsekula Pachiweru kwa zaka zitatu tsopano. +Iye adati chipatalachi chili ndi ogwira ntchito asanu okha, omwe atatu aiwo ndi anamwino, ndipo awiri ndi olembera odwala. +Mkulu wachipatalachi amatiyankha kuti amapita kutchalitchi Pachiweru ndipo chipatala satsekula. Koma ife timadabwa kuti bwanji sauza ena omutsata kuti azithandiza anthu patsikulo? adatero iye. +Popheramphongo, Mfumu yaikulu Mkanda idati kafukufuku wake wasonyeza kuti chipatalachi sichitsekulidwa Pachiweru ndipo odwala ochokera mzipatala zazingono zozungulira deralo monga Kazyozyo, Kaligwazanga ndi Gumba, amawapatsa bedi podikira Lolemba. +Odwala akabwera Lachisanu, samawaona tsiku lomwelo. Iwowa amapatsidwa bedi mpaka Lolemba. Sitikudziwa kuti nkutani. Chaka chatha tidapempha kuti atichotsere, koma tangodabwa kuti wagoneranso. Pano nzeru zatha, idatero mfumuyo. +Iyo idati masiku ena mkuluyo amatha kungothandiza owadziwa kapena munthu akamkomera mtima. +Iye adati nkhaniyi idakafika ku likulu kwa bomalo ndipo adamkhazikako bwalo pamaso pa akuluakulu a boma ndi dotolo wamkulu wa bomalo yemwe pano adasamukira ku boma lina. +Atsekera wogwiririra Gogo wa zaka 80 Bambo wa zaka 54 yemwe adagwirira gogo wa zaka 80 ku Dowa amulamula kuti akaseweze zaka ziwiri ndi theka atamupeza wolakwa pamlanduwu. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Khoti la Msongandewu, lomwe lili ku Mvera mbomalo lidapereka chilangocho kwa mkuluyo, Biwi Ephraim wa zaka 54, koma anthu ozingwa ndi zimene adachitazo ati chigamulocho nchofooka. +Anthu a mmudzi mwa Nyemba kwa Mfumu Yaikulu Chiwere mbomalo adaima mitu ndi zomwe Ephraim adachita pogwiririra gogoyo potengera danga kuti gogoyo adaledzera. +Chomwe chaimika mitu anthuwa nchakuti bamboyu ali pabanja ndipo ali ndi ana 7. Anthu a mmudzimo ati sakumvetsa chomwe chidamukopa bamboyu kunyazitsa gogoyo. +Mmodzi mwa anthuwo, Joel Machira, adati: Izi zikachitika, timaganizira masilamusi kapena kukhwima chifukwa munthuyu ali ndi banja ndipo ngati mthupi munatentha akadatha kupeza mpumulo kunyumba kwake. +Kaponda: Gogoyo adapita kokamwa Ndipo Rose Thodwa adati mkuluyo adayenera kulandira chilango chokhwimirapo. +Uku nkuvula mtundu chifukwa gogo wa zaka 80 ndi mtsitsi wa anthu ambiri ndiye kumupanga chipongwe nzosamveka, adatero Thodwa. +Mneneri wa polisi mbomalo, Richard Kaponda adati patsiku la chipongwelo, gogoyo adapita kukamwa mowa mmudzi mwa Chiponda mdera lomwelo ndipo pobwerera, bambo wachipongweyo amamuzemberera. +Atafika mmudzi mwa Chifisi, adambwandira gogoyo nkumukokera patchire pomwe adamuchita chipongwecho ndipo achipatala cha mishoni cha Mvera adatsimikiza kuti adagwiriridwa, adatero Kaponda. +Ephraim amamuzenga mlandu wogwiririra zomwe zimatsutsana ndi ndime 132 yamalamulo ndipo iye adakana mlanduwo koma woyimira boma Sergeant Benedicto Mathambo adabweretsa mboni zitatu mkhothimo. Iye adati chilango chokhwimitsitsa chimene akadalandira nkukhala kundende moyo wake onse. +Wolakwayo adapempha ogamula mlanduwo majisitileti Amulani Phiri kuti amuganizire pogamulapo chifukwa ali ndi banja lofunika chisamaliro komanso ndi wamkulu. +Popereka chigamulocho, Phiri adati zomwe adanena Mathambo nzomveka komanso potengera umboni omwe udaperekedwa mkhotimo, Ephraim akuyenera kukakhala kundende zaka ziwiri ndi theka akugwira ntchito yakalavulagaga. +Milandu mbweee! mu 2016 Chapita chaka cha 2016 chomwe dziko lino lidaona ina mwa milandu ikuluikulu ikulowa mmabwalo a milandu ndi kuweruzidwa. +Umodzi mwa milanduyi udali wa yemwe adali nduna ya za chilungamo zaka zapitazo yemwenso ndi kadaulo pa malamulo, Ralph Kasambara. +Kasambara, pamodzi ndi Pika Manondo komanso MacDonald Kumwembe adayankha mlandu woti adakonza chiwembu chofuna kupha mkulu woyendetsa ndondomeko za chuma wakale Paul Mphwiyo mu 2013. +Kasambara (wasuti) kupita kundende Mwezi wa July, bwalo la milandu lalikulu mumzinda wa Lilongwe lidamupeza Kasambara wolakwa pamlanduwo ndipo mwezi wa August adagamulidwa kukasewenza jere kwa zaka 13. +Manondo ndi Kumwembe adagamulidwa kukasewenza jere zaka 15 ndi 11 aliyense pa milandu iwiri: yochita upo pofuna kupha komanso mlandu wofuna kupha Mphwiyo panja pa nyumba yake ku Area 43 mumzinda wa Lilongwe usiku wa September 13 chaka cha 2013. Milanduyi asewenza paderapadera. Pamodzi, Mandondo ndi Kumwembe asewenza zaka 26. +Mlanduwutu tsopano uli kubwalo la apilo. +Mchakachi tidaonanso fisi wa ku Nsanje, Eric Aniva, akukalowa mchitokosi pogona ndi amayi 104 mbomali. +Aniva yemwe ndi wa zaka 45, wochokera mmudzi mwa Tosina kwa mfumu yaikulu Mbenje, mbomalo adapezeka wolakwa pa milandu iwiri yokhudza kuika miyoyo ya ena pachiswe potsatira miyambo ya makolo. +Aniva adanjatidwa pomwe adauza wailesi ya atolankhani a British Broadcasting Corporation (BBC) za ufisiwu mwezi wa July. +Ngakhale Aniva adaukana mlanduwu pa November 22, woweluza milandu Innocent Nebi adamugamula kukasewenza zaka ziwiri ku ndende. Padakali pano, womuyimira Michael Goba Chipeta wachita apilu. +Nawo mlandu wa mtsogoleri wagulu lomenyera ufulu wolanda malo mmaboma a Thyolo ndi Mulanje la Peoples Land Organisation (PLO) Vincent wandale udali mkamwamkamwa mwa anthu mchakachi. +Alandira K14 biliyoni yotukulira maphunziro Maiko ndi mabungwe omwe amathandiza boma ati apereka thandizo la K14 biliyoni ku unduna wa zamaphunziro zotukulira maphunziro msukulu za pulayimale. +Lonjezoli lili mumgwirizano wa pakati paboma la Malawi ndi maiko a Norway ndi Germany kudzanso banki yayikulu padziko lonse ya World Bank ndi bungwe la United Nations Childrens Fund (Unicef). +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Haugen: Tiyamba chaka chino Mbali ziwirizi zidasayinirana mgwirizanowu Lachitatu pasukulu ya pulayimale ya Muzu mboma la Lilongwe ndipo oyimirira mayiko ndi mabungwewa, Kikkan Haugen, yemwe ndi kazembe wa dziko la Norway adati ndalamazi ziyamba kufika chaka chino. +Gawo loyamba libwera chaka chino ndipo lichokera ku Norway, World Bank ndi Unicef ndipo gawo lachiwiri lidzabwera 2018 ndipo lidzachokera kudziko la Germany, adatero Haugen. +Iye adatsindika kuti izi sizikutanthauza kuti maiko ndi mabungwewa ayambiranso kupereka thandizo lomwe ankapereka ku bajeti ya Malawi ndipo adasiya pa zifukwa zosayendetsa bwino ndalama za mbajeti. +Mkulu wa bungwe la mgwirizano wa mabungwe omwe amayanganira za maphunziro, Benedicto Kondowe, adati nkhaniyo ndi mayeso aakulu ku unduna wa zamaphunziro ndi boma la Malawi. +Oyendetsa pulogalamu ya thandizo la mumgwirizanowu akuyenera kuzindikira kuti tsogolo la thandizo lina mtsogolo likhala mmanja mwawo chifukwa ntchito zawo ndizo zingakope mayiko ndi mabungwe ena kuti alowererepo, adatero iye. +Nduna ya zamaphunziro ndi sayansi Emmanuel Fabiano adati boma la Malawi kudzera muunduna wake lionetsetsa kuti thandizoli labweretsa kusintha mmaphunziro a ku pulayimale mdziko muno. +Boma, sukulu ndi makolo atenga nawo mbali pachitukuko chilichonse chomwe chikhazikitsidwe mmapologalamu a mumgwirizanowu ndiponso liziyesetsa kupereka upangili ndi zofunika kuwonjerapo mmapologalamuwo, adatero iye. +Sindidalakwe, watero Wandale Mtsogoleri wa gulu lomenyera ufulu wolanda malo mmaboma a Thyolo ndi Mulanje la Peoples Land Organization (PLO) Vincent Wandale, yemwe bwalo la milandu la Blantyre Magistrate lidampeza wolakwa pamilandu itatu ndi kumugamula kuti akhale miyezi 18 asadapalamulenso, wati iye sadalakwe ndipo achita apilo kubwalo la milandu lalikulu. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Wandale, yemwe pa 1 September chaka chino adamemeza anthu kukalowerera esiteti ya tiyi ya Conforzi mboma la Thyolo ati ponena kuti malowo ndi a makolo awo, adapezeka wolakwa pamilandu yolowerera malo a eni popanda chilolezo komanso kupanga upo woipa. +Ndipo Lachiwiri lapitali , Wandaleyu adagamulidwa ndi woweruza milandu wamkulu pabwalo la milandu la Blantyre, Thokozani Soko. +Polankhula ndi Msangulutso Lachinayi lapitali, Wandale adati sadakhutire ndi chigamulocho chifukwa padali zolakwika zingapo. +Ine ndikukhulupirira kuti sindidalakwe ndipo pachifukwa ichi, ndikasuma kuti bwalo lalikulu liunikenso chigamulo chomwe adandipatsa. Pali zinthu zina zingapo zomwe sadaziyanganitsitse poweruzapo ndipo ndikukhulupirira kuti bwalo lalikulu likaziunika zimenezi, adatero Wandale. +Iye adati mwachitsanso, bwaloli silidampeze kuti upo omwe adapangitsa udali utiuti ndipo ankatani. Iye adati izi zidalibe umboni weniweni. +Ndipo chachiwiri iye adati abwaloli sadapenzenso umboni kuti iye adapita nawo kuesiteti ya Conforzi ati kaamba koti iyeyo kudalibe kumaloko patsikulo. +Chachitatu ndi choti ifetu anthuwa tidawalembera kalata kuwadziwitsa za dongosolo lathu, koma iwowa sadayankhe zomwe kwa ife tidatanthauzira kuti ativomereza kukalowa kumalowa. Sitikumvetsa chifukwa chomwe abwalo akunenera kuti tidaphwanya lamulo pomwe anthu tidawadziwitsa bwino lomwe, adalongosola motero. +Ndikukhulupirira kuti sangakandilowetsenso jere chifukwa mlanduwu ngwaungono komanso palibe adagwiritsa ntchito malo a Conforzi komanso nkhaniyi ndi ya gulu, adatero Wandale. +Polankhulapo, mlembi wa bungwe loona za malamulo mdziko muno la Malawi Law Society (MLS), Khumbo Soko, adati Wandale ngati munthu wina aliyense ali ndi ufulu wokasuma ngati sadakhutitsidwe ndi chigamulo. +Chonona chifumira kudzira Tikamakamba za kufunika kuti pasamakhale kusiyana pa mwayi womwe amayi ndi abambo akupatsidwa, titamakumbuka za mwambi uwu wakuti chonona chifumira kudzira. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Izitu zikutanthauza kuti kusintha kwenikweni pakhalidwe la anthu kwagona pa momwe anthu akuleredwera mmakomo mwawo, mmadera momwe tikukhala, mmipingo komanso kusukulu. Chimodzimodzinso nkhani ya kuthetsa nkhanza mmabanja komanso nkhanza zina zomwe anthu amakumana nazo kaamba koti ndi aakazi kapena aamuna, tikumbuke ndithu kuti nthawi youmba khalidwe la munthu ndi nthawi yomwe akukula. +Mwachitsanzo, anthu ambiri-abambo ngakhalenso amayi-amene amakhala ndi mtima woderera amayi, amakhala kuti adakula pakati pa chikhalidwe chomwe chimaonera amayi pansi. Anthu oterewa amavuta kuti akhale pansi pautsogoleri wa mzimayi chifukwa amangoona kuti munthu amene akuwalamula sakuyenera kutero. +Chikhalidwe cholakwikachi chimakhala chokhazikika mmitu mwawo ndipo kukonza kwake akakula kumakhala kovuta. Tsono udindo wambiri wokonza makhalidwe olakwikawa uli mmanja mwa makolo poonetsetsa kuti nzika zomwe mukulera zikhale ndi zikhulupiriro komanso makhalidwe oyenerera osapondereza, kuzunza kapena kuderera anthu ena kaamba ka momwe adabadwira. +Amayi amene azunzika mmabanja ndipo ali ndi ana aamuna, akhoza kuonetsetsa kuti mwana amene akulera uja asadzakhale ngati bambo ake kuti adzazunzenso mkazi wake akakula. Ana aamuna aphuzitsidwe kulemekeza munthu wamayi. Adziwe kuti kusiyana kwawo ndi munthu wamkazi kwagona pa kaumbidwe ka ziwalo zawo pakabadwidwe. +Zikakhala nzeru ndi machitachita ena palibe kusiyana. Auzidwe ana aamuna kuti mzimayi ndi muthu ngati iwo. Si chida chongoti wina akafuna agone nacho kapena kumamunyozetsa kumamuimbira miluzi akamayenda mmisewumu. +Chimodzimodzinso ana akazi tiwaphunzitse kuti ali ndi kuthekera kofikira komanso kukhala chilichonse chomwe angafune pamoyo wawo. Tiwaphunzitse atsikana kuti asadalire thumba la munthu wammuna chifukwa chomwe bambo akuchita kuti apeze ndalama pakhomo iwonso akhoza kupanga. +Mtsikana asalunjike nzeru zake pa thupi lake. Pali luso, nzeru ndi zinthu zina zomwe anadalitsidwa nazo kuti zipindulire iye komanso dziko. +Aphunzitsidwenso mwana wamkazi kuti asalole munthu aliyense kumukokera pansi kapena kumuchitira nkhanza-angakhale mbale kaya mwamuna wake. Mwanayo auzidwe akali wamngono kukana ndi kusapirira mtundu uliwonse wa nkhanza. +Kuvulaza namfedwa Ndinali pa maliro ena masiku apitawa komwe amfumu adaganiza zokhutula nkhawa zawo za anamfedwa tili kumanda. Amfumuwo adati sadakondwe ndi momwe bambo wa malemu ankathamangira thamangira pamaliro mmalo mosiira ena kuti amuthandize. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Polankhula, amfumuwa adadzudzula bamboyo akuti chifukwa ali ndi chizolowezi chochita zinthu mwayekha posafuna kuthandizidwa ndi ena. Aka sikanali koyamba kumva anamfedwa akudzudzulidwa mokhadzula mokhudzana khalidwe lawo pamudzi. +Ena amadzudzulidwa kaamba kosapezeka maliro akagwera anthu ena. Ena amadzudzulidwa chifukwa chophonya ndondomeko kapena miyambo ina yokhudza maliro. Ndaonaponso anamfedwa ena ataphikiridwa nsima pamaliro nkuwasiira kuti adye okha ati chifukwa iwo akapita kumaliro a ena sadya chakudya. +Pamene anthu tikukhala mmagulu, sipangalephere wina kulakwitsa kapena kulakwira ena. Nthawi zina pa zifukwa zomwe sitidziwa ena sachita nawo zoyembekezeka pagulu ngati kudya nsima pamaliro. Osakhala kuti akudana ndi nsimayo koma anthufe timayenda ndi matenda osiyanasiyana omwe nthawi zina salola ena kumangodyapo chisawawa. +Ena kungodya za mchere kaya mafuta ndiye kuti aputa zosaputa mthupi. Sangakwanitse kulengeza za matenda awo kwa aliyense kuti awamvetsetse, nthawi zina kachetechete amangopewa zakudya zomwe sizinaphikidwe mwa dongosolo lomwe adapatsidwa kuchipatala. +Yakhota pangono nkhaniyi, apa pagona nkhani lero ndi pa funso ili kuti nchi chifukwa chiyani amfumu ngakhalenso atsogoleri a mmadera ndi midzi yomwe tikukhala amafuna kumudzudzula namfedwa panthawi imene akumva kale kupweteka kotaya mbale wake? Amene mwaferedwapo mukudziwa kuwawa kwa imfa. +Anatchezera Chikondi amatero? Agogo, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndine mtsikana wa zaka 20 ndipo ndili kukoleji. Ndili ndi chibwenzi chomwe tidagwirizana kuti tidzamange banja mtsogolo muno. Mnzangayu amati akufuna kuti adzandidziwire mbanja chifukwa akayamba kundigona panopa atha nane filimu. Ndiye akuti poti iyeyu ndi munthu pena zimavuta ndiye akuti akufuna apeze mkazi woti azigonana naye popewa kugonana ndi ine kuti inyeyo adzandikwatire. Kodi kumeneku ndi kukonda? Ndithandizeni, agogo, nditani. +Ndine L, Lilongwe Wokondeka L, Bwenzi lakolo ndi munthu wachilungamo, inde, koma chilungamo chake chaonjeza. Munthu wotere osamukhulupirira chifukwa ndi kamberembere. Iyeyu wanena chinthu chanzeru kwambiri kuti pakalipano musamagonane chofukwa akuopa kuti akatero atha nawe chilakolako chifukwa wakudziwa. Koma akuti akufuna apeze mkazi wina wapambali kuti azikapumirako poti iye ndi munthu, nanga iwe wakuuza kuti nawe utha kupeza wina woti uzicheza naye pamene mukudikira kuti mudzakwatirane? Akunama ameneyo; akufuna kuti azioneka ngati munthu wokhulupirika pomwe ndi wachimasomaso ndi akazi ena. Tikamati kudzisunga ndi nonse awiri, osati wina aziti mnzangawe udzisunge koma ine ndikayendayenda. Kunjaku kwaopsatu, ndiye wina azipanga dala zachibwana ngati zimene akunenazo, si zoona ayi. Ngati ndi wachilungamo, iyenso ayenera kupirira kuchilakolako cha thupi kufikira tsiku lomwe mudzalowe mbanja. Koma ngati adayamba kale zogonana ndi akazi ena, mchitidwe umenewo sadzausiya. Ndiye, kunena zoona, mwamunayo sali woyenerera kumanga naye banja chifukwa alibe chikondi chenicheni ndi iwe. Amati mbuzi ikalawa mchere sigwirika! Safuna zoyezetsa Anatchereza, Ndakhala ndili pachibwenzi ndi mtsikana wina kwa chaka chimodzi ndipo timakondana kwambiri. Ndine Mkhristu ndipo ndikhulupirira kuti sibwino kumagonana ndi wachikondi wako musadalowe mbanja lomanga. Ndakhala ndikumva malangizo oti masiku ano ndi bwino kukayezetsa magazi musanaganize zolowana, koma mnzangayu nditamuuza zimenezi adati ine zimenezo ndiye ayi. Kumufunsa chifukwa chake adati ineyo ngati ndikudzikaikira ndipite ndikayezetse, osati iyeyo. Akuopa chiyani? MJ Lilongwe Odi MJ, Akuopadi chiyani ameneyo? Pati bii, pali munga, ife akale timatero. Chilipo chimene akuopa chifukwa akanakhala kuti ali bwinobwino, si bwenzi akuchita kukanira patalitali kuti ine toto, pita wekha. Kudziwa mmene munthu ulili usanalowe mbanja ndi chinthu chabwino kwambiri, makamaka masiku ano pamene kuli mliri wa kachilombo ka HIV/Aids. Mundimvetse bwinobwino pamenepa: si kuti munthu akapezeka ndi HIV ndiye kuti sayenera kukwatira kapena kukwatiwa, ayi. Munthu aliyense ali ndi ufulu wokhala pabanja, koma zimakhala bwino kudziwa mmene mthupi mwako mulili pofuna kukonza tsogolo la banja lanu. Ngati wina apezeka ndi kachilombo kapena matenda ena kumphasa mumadziwa chochita pofuna kudziteteza kuti nonse mukhale moyo wathanzi. Komanso ngati mukufuna mwana mbanja mwanu madotolo amadziwa njira zokuthandizirani kuti mwana wanu asatenge nawo kachilomboko. Chachikulu ndi chikondi pakati panu-pali chikondi palibe mantha. Mufotokozereni wokondedwa wanuyo zimenezi kuti amvetsetse, koma ngati akumenyetsa nkhwangwa pamwala, musiyeni ameneyo, muyangane wina amene angakumvetsetseni pankhani yoyezetsa magazi. +Nsalu ya lekaleka Anatchereza, Ine ndi mwamuna wanga takhala pabanja zaka ziwiri ndipo nthawi yonseyi takhala tikugwiritsa ntchito njira zolera chifukwa mwamuna wanga amati nthawi yoti tikhale ndi mwana sinakwane-titoleretolere kaye kuti tisadzavutike tikadzakhala ndi mphatso ya mwana mnyumba mwathu. Kunena zoona zimene amati titoleretolere kaye sindikuziona, komanso anthu kunjaku ndiye akumatiseka ndi kumatinyogodola kuti sitibereka. Ine ndiye ndatopa nazo zimenezi. +KB Mzimba KB, Nkhani yanu ndi yovuta kuimvetsa, komabe ndikuthandizani. Choyamba, kodi pamene mumagwirizana zomanga ukwati wanu, mudayamba mwakhala pansi nkukambirana za mapulani anu pa nkhani yokhala ndi ana kapena izi munagwirizana mutalowana kale? Ndikufunsa chifukwa ukwati ndi anthu awiri. Ine ndikuona ngati mwamuna wanu chilipo chimene sakufuna kuti mudziwe ndipo akunamizira kuti nonse mukulera. Zaka ziwiri mukutolera za mwana? Mukutolera chiyani? Mwanena kale kuti palibe chimene mukuona kuti mwatolerapo mpakana pano. Mumufunse ameneyo kuti nthawi yakwana tsopano kuti mulandire mphatso yomwe mwakhala mukuiyembekeza ija. Mumuuze kuti simupanganso zolera koma zenizeni, mumve chimene ayankhe. Ngati pali vuto lomwe akuchita nalo manyazi kukuuzani, mumuuze kuti asaope chifukwa inu ndi thupi limodzi-mavuto ake ndi anu omwe. Kuli asinganga odziwa kusula kunja kuno! Akakanika, kuchipatala amathandizanso! Ndani safuna mwana? Sakundilankhula Zikomo Anatchereza, Ndili pabanja ndi mkazi wina ndipo timakondana kwambiri. Koma akwawo sagwirizana nawo ndipo ngakhale akumane panjira salankhulana. Ngakhale ine ndikawalankhulitsa sandiyankha. Ndichitenji chifukwa ndikuopera mawa atadwala kapena kumwalira kumene. Thandizeni. +Luso losema ziboliboli Luso longosema lafika apa? Basitu ntchito zake Namalenga kuti nafenso tikhale ndi popezera ndalama. +Escom in free-for-all fuel scam Wait gets longer Secrecy over party funders Malo anu amenewa? Amenewa ndi malo anga komanso mkulu wanga amene ndikugwira naye ntchitoyi. +Mudatsegula liti malo ano? Alick kuonetsa chipembere chomwe adasema Adatsegulidwa mu 2012, koma ndidayamba kusema ziboliboli mu 1998. Nthawiyo ndimagwira ntchitoyi ndikukhala ku Mua kenaka ndimapangira kunyumba kwanga. Mu 2012 ndi pamene timatsekula malo ano. +Mumasema chiyani? Timasema mtundu ulionse wa zinyama omwe munthu akufuna, chifaniziro cha munthu, mayi Maliya, chifaniziro cha anthu a mtundu wa Chingoni, galimoto ndi zina zambiri zomwe sindingakwanitse kuzitchula zonse. +Mukugwiritsa ntchito mtengo wanji? Pali mitengo yambiri yomwe anthu amagwiritsa ntchito koma ife timakonda mtengo wa mtumbu. +Mumagwiritsira zida ziti popanga katunduyu? Mukakadula mtengowo, mumayenera kuyamba kusema ndi sompho, chikwanjenso chimafunika, tchizulo, sandpaper, polish ndi zida zina ndi zina kuti chomwe tikusemacho chioneke bwino. +Ndaona chifaniziro cha nyama ya chipembere, zimatenga masiku angati kuti mupange? Nanga mumagulitsa bwanji? Pakutha pa sabata ziwiri timakhala tamaliza kupanga chipembere. Chimenechi chikugulitsidwa K15 000. Chifaniziro cha mayi wa mtundu wa Chingoni timagulitsa K20 000. +Khirisimasi ya Niko Nthawi ija yafikanso. Niko adali pa Wenela tsiku limenelo Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Abale anzanga, ndikuthokoza Mulungu amene wandilola kuti ndifike tsiku la lero! Komatu palibe munthu waimva kukoma Khirisimasi kukoma ngati Niko. Mwamuiwala uja ankathandiza gogo uja kuwerenga zaka zambirizo? Mwamuiwala Niko ankakhala kumbuyo kwa gogoyo makamaka tsiku lija adandipeza ndikulima kwathu kwa Kanduku? Tsonotu sindinena za Tomasi Akwino wanzeru zozana. Sindinganene za Niko yemwetu ngakhale Chichewa chake nchozama zedi. +Niko, mwaitha. Mwachoka kumpando wosunga zisinsi, mwafika kumpando woulula zinsinsi. Mukamva bwa? adafunsa Abiti Patuma. +Mwanaaaa! Nkuuze inetu ndili okondwa zedi. Mukakhala enanu mukadawerenga 1 mpaka 10 koma ine ndikuti penda, penda kuwiri, mwanangu, wansiira kansonjo, njonjonjo, mbiringo, njoli, sansamera, khumi lagwa, adayankha Niko. +Zinthutu zimasintha. Malisani, Malisani! Zoona Moya Pete nkumutaya Malisani? Ndazitaya ndekha. Chilungamo chidaphetsa msemamitondo, adatero Malisani atafika pamalo paja timakonda. +Gervazzio adaika nyimbo ya Fumbi Jazz Band: Mmene ntchito yanga yatha Mwayesa nkhani? Funani ina nkhani anzanga Sankhani ina, anzanga! Palibe icho ndidatola. Kodi si uyu Maliseni adasambwadza Lazalo Chatsika masiku apitawo? Kodi siyemweyu ankanena kuti Moya Pete akukumana ndi anthu ofunika? Kodi si yemweyo zidamutsamwa atanena kuti Moya Pete ali bwino chonsecho atabwera mwini wake adatiuza tonse pa Wenela kuti nyamakazi inamugwira ntchafu? Kodi Niko, izi adalankhula Chatsika mukuti nazo bwanji? Nanga enatu akuti akusankhani kuti muchititse nkhani youlula zinsinsi ikhale yovuta, mukutipo bwanji? adafunsa Abiti Patuma. +William the Conqueror, whose cause was favoured to by Moya Pete, requested quiet clearly stated sequentially created when Thomas Tatertoot took taut twine to tie ten twigs to two tall trees, adayankha Niko. +Sindidatolepo kanthu. Mwina chifukwa ndidali kulingalira ngati mkazi wanga wokondeka Nambe walandira kuponi. +Kuthimathima kwa magetsi kwakhudzanso akumidzi Ndi Lolemba mmbandakucha wa pa 12 September, nthawi yangokwana kumene 4 koloko koma magetsi azima kale mboma la Mulanje. Chiyembekezo nchoti posakhalitsa ayaka. +Gulu la alimi lopanga tsabola wa Zikometso Hot Chilli Sauce, maso akudikira kuti mwina magetsi ayaka nthawi iliyonse. Poyembekezera, asakaniza kale tsabola kuti magetsi akangoyaka ayambe kuphika mmakina awo. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Akadadziwa akadaphika therere! Magetsi sadayake tsiku lonse. Pofika 7 koloko mmawa wa Lachiwiri, magetsi kuli chuu, zomwe zapangitsa kuti akataye zosakanizazo. +Umu ndi momwe zikukhalia kwa anthu akumudzi amene sangakwanitse kupeza injini ya magetsi (generator). +Makampani a alimi akulephera kuyendetsa malonda awo, zinthu zasokonekera chifukwa cha kuthimathima kwa magetsi, komwe kukulowa mwezi wachiwiri tsopano mdziko muno. +Nalo bungwe lopanga ndi kugulitsa magetsi la Escom laneneratu kuti mavutowa anyanyira miyezi ikubwerayi chifukwa cha kuchepa kwa madzi omwe amapukusa makina opangira magetsi ku Nkula ndi ku Tedzani mumtsinje wa Shire. +Monga akufotokozera wachiwiri kwa mkulu wa Zikometso, Amos Ambali, pasabata amapanga mabotolo a tsabola 2 100, koma pano akupanga osaposera 500. +Timagwira ntchito Lolemba mpaka Lachisanu, koma masiku onsewa kukukhala kopanda magetsi. Mapeto ake tayamba kugwira usiku wokhawokha komanso Loweruka masana pamene magetsi akumayaka. +Sizikupanganika, pena kukukhala kopanda magetsi tsiku lathunthu, zomwe zasokoneza bizinesi yathu. Kangapo konse tataya tsabola patatha masiku awiri popanda magetsi kupangitsa kuti tsabola wathu aonongeke, adatero Ambali. +Nawo a Talimbika Agro-Processing and Marketing Cooperative Society, amene amapanga mafuta ophikira a Sunpower mboma la Salima, akuti magetsi akazima, amagulula makina awo ndi kuchotsa mpendadzuwa yense. +Fanny Jodani ndi mmodzi mwa akuluakulu pa Talimbika ndipo akuti patha miyezi iwiri magetsi akuzimazima ndipo tsiku lililonse akumazima isadakwane 4 koloko nkumayaka 6 madzulo. +Apapa tayamba kugwira ntchito usiku, komabe zikuvuta chifukwa pena kukumakhala kopanda magetsi. Magetsi akazima sitigwira ntchito ndipo timagulula makina athu, kuchotsa mpendadzuwawo, adatero. +Talimbika imapanga malita 500 patsiku ngati magetsi akuyaka, koma pano tsiku likutha osapanga mafuta. +Ali ndi antchito oposa 11 amene akufunika malipiro, kodi akumawalipira bwanji? Mkulu wa Talimbika, Pharison Chiwoko, akuti ili ndi vuto lalikulu. +Magetsi akamayaka bwino, timapanga ndalama yoposa K3 miliyoni pamwezi. Mwezi unowo ngakhale K1 miliyoni sikwana. Timaononga K700 000 kuti tilipire antchito. Mutha kuona kuti mwezi uno ngati anthu alandire ndi mwayi, akutero Chiwoko. +Nako ku Dowa zinthu sizili bwino. Watson Kamchiliko mkulu wa Madisi Agro-Processors Cooperatives, omwenso amapanga mafuta ophikira, wati pali mantha kuti angachotse antchito ena ngati sizisintha. +Timapanga malita 2 000 patsiku. Lero zasintha, tikumapanga malita 2 000 pasabata, bizinesi yasokonekera. Tili ndi ogwira ntchito amene akulandira K150 000, kodi awa tingawalipirenso? adatero Kamchiliko. +Nako kuchigayo kwasokonekera. Kamchiliko akuti anthu akugona kuchigayo kudikira kuti magetsi ayake pa boma la Dowa. +Pena amayaka cha mma 10 koloko usiku, anthu amagona kuchigayo kuti akayaka agaitse, adatero. +Kwa T/A Phambala mboma la Ntcheu, eni zigayo za dizilo apezerapo mwayi ndi kuzimazima kwa magetsi pamene akweza mtengo kuchoka pa K300 thini kufika pa K350. +Koma uthenga kuchokera kubungwe la Escom sukupereka chiyembekezo kwa anthuwa. +Mkulu wa bungweli, John Kandulu, akuti izi zikhala zikuchitika kuyambira mwezi uno mpaka December pamene mvula idzakhale itayamba. +Kandulu akuti izi zili chonchi chifukwa mlingo wa madzi a mumtsinje wa Shire ndi wotsika ndipo kutsikaku kupitirira pokhapokha mvula itayamba. +Chifukwa cha izi, tingokwanitsa kutapa 135 megawatts mmalo mwa 361 megawatts zomwe zichititse kuti magetsi akhale akuzimazima, adatero Kandulu. +Tidasala masiku 52 kuti Mulungu atiunikire Nthawi zambiri, anthu timatenga banja ngati sitepe pamoyo wathu basi koma tikalingalira momwe banja la mbusa komanso mlembi wa mkulu wa mpingo wa CCAP Reverend Vasco Kachipapa Banda ndi mkazi wake Madalitso Nyoli, mibadwo yobwerayi idzazindikira momwe banja la umulungu limakhalira. +Awiriwa akuti adakumana mu 1992 onse atasankhidwa kupita kusukulu ya sekondale ya Mitundu ndipo chikondi chawo chidayamba mu 1994 koma uku sikudali kuyamba kwa banja poti zambiri zidadutsapo. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Rev. Kachipapa adati mizati itatu ndiyo idagwira ntchito kuti awiriwa atseguke mmaso kutidi adalengedwa kudzakhala limodzi ndi kutumikira Chauta ngati bambo ndi mayi komanso odyetsa ndikusamala nkhosa zake. +Kachipapa ndi Madalitso: Lero ndi banja Mzati woyamba, ineyo ndidadwala tikadali kusukulu mpaka ndidapita kunyumba. Nditapeza bwino nkubwerako, Madalitso adabwera kudzandizonda ndipo aka sikadali komaliza. Pamenepa ndidazindikira kuti ndi umunthu weniweni, adatero Kachipapa. +Iye adati chikondichi sichidasanduke mapeto azonse ayi koma chiyambi cha kudzifunsa ndi kupempha utsogoleri wa Mulungu. +Mchaka cha 1997, tonse awiri tidayamba mapemphero ndi kusala kwa masiku 52 (Loweruka lokhalokha) kupempha Mulungu kuti atiunikire ngatidi tidali oyenera kukwatirana. Ndi mzati wachiwiri ndipo mzati wachitatu udali nthawi yomwe ine ndimapanga maphunziro a zaubusa ku Zomba, mkazi wanga adali atayamba kale ntchito ndipo adandithandiza kupereka malowolo ake omwe, adatero Kachipapa. +Iye adati Chauta atavomereza zonse, ndondomeko zoyenera zidatsatidwa kufikira nthawi ya chinkhoswe mchaka cha 1998 ndipo kenako ukwati woyera ku Ntchisi CCAP. +Ndimakonda mkazi wanga kwambiri chifukwa cha mtima wake wabwino, amakonda kupemphera kwambiri ndipo simkazi wanga chabe koma mzanga muuzimu, adatero Kachipapa. +Nawo mayi a kunyumba akuti (Madalitso) akuti abusawa ndi bambo wabwino wokonda banja lawo ndi wodziwa kusamala. +Ndi bambo abwino kwambiri odziwa udindo wawo ndiokonda banja lawo komanso kusamala ana awo. Timapemphera limodzi, kuyenda limodzi, kudya limodzi mwachidule timapangira zinthu limodzi, adatero mayiwo. +Apolisi akupitirirabe kuphwanya malamulo A polisi atatu agwidwa ndi kutsekeredwa mchitolokosi chawo chomwe mumzinda wa Zomba powaganizira kuti adathandizira mayi wina yemwe akuti adaba ndalama mdziko la South Africa kutuluka mchitolokosi. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Apolisiwa ndi Sub Inspector Khudze, Sergeant Mbalame ndi Mankhwala omwe akuganiziridwa kuti adathandiza mayiyo yemwe akuti adaba ndalama zokwana pafupifupi K17 miliyoni kwa bwana wake mdzikolo. +Izi zidachititsa apolisi a dzikolo kulumikizana ndi a dziko lino omwe mwaukadaulo wawo adamugwira mayiyo, koma ena mwa apolisi omwewo akuti adapezerapo mwayi wotakata ndipo anamutulutsa mwamseri. +Ndipo ku Zomba konko wapolisi wina ,yemwe akungodziwika kuti Kalipinde, adamangidwanso poganiziridwa kuti adachita zakatangale. +Izitu zachitika patangodutsa sabata imodzi wapolisi winanso, Constable Kamoto atatsekeredwa mchitolokosi cha polisi ya Soche mumzinda wa Blantyre pomuganizira kuti adasowetsa mfuti ataledzebwa pamalo ena omwera mowa. +Pakadalipano apolisi akuti mfuti idasowayo idapezeka. +Ngakhale izi zikuchitika, anthu mdziko muno amadalira apolisi pankhani yosungitsa lamulo komanso chitetezo. +Kwa zaka zingapo tsopano, apolisi akhala akupezeka ndi milandu yosiyanasiyana, monga kulowetsa anthu omwe alibe ziphaso mdziko muno podzera njira zosavomerezeka, umbava ndi umbanda komanso kuzunza ena mwa anthu omwe amagwidwa akuyenda usiku. +Ndipo nthawi yonseyi, boma komanso akuluakulu awo akhala akutsimikizira mtundu wa a malawi kuti izi zikhala mbiri yakale kaamba koti kagwilidwe ntchito ka apolisiwa kanaunikidwanso. +Polankhulapo mneneri wa polisi mdziko muno James Kadadzera adavomereza kuti ena mwa apolisi akupitirizabe kuswa malamulo ndi kusasunga mwambo. +Kadadzera adati koma akuluakulu a apolisiwa sakusekerera izi ndipo akulanga opezeka akuswa malamulowo pogwiritsa ntchito njira ziwiri. +Iye adati ena akumalangidwa pogwiritsa ntchito njira zawo za polisi pomwe ena akumalangidwa pogwiritsa ntchito malamulo a dziko lino. +Mwachitsanzo apolisi anayi omwe sindiwatchula maina awo, adatsekeredwa mumzinda wa Zomba titalandira dandaulo lakuti adakhudzidwa ndi zakatangale, ndipo alangidwa potengera malamulo a dziko lino, pomwe Kamoto akulangidwa pogwiritsa ntchito malamulo athu, adatero Kadadzera. +Iye adakana kuyankhulapo mwatsatanetsatane za milandu ya anayiwa. +Kadadzera ngakhale izi zili chomwechi, chiwerengero cha apolisi opezeka akupalamula chikuchepera. +Koma musaiwale kuti ngakhale alipo apolisi omwe akugwira ntchito yawo molimbika ndi modzipereka, aliponso ena omwe akuswa malamulo. Choncho tili ndi nthambi yoyangana kagwiridwe ka ntchito mwaukadaulo ya Profession Standard Unit (PSU) yomwe ikulimbikitsa kusunga mwambo mupolisi, adatero Kadadzera. +Ndipo nduna ya za mdziko Grace Chiumia adati atsirirapo bwino ndemanga pankhanizi akamva tsatanetsatane wa nkhani zomwe zidachitika ku Zombazi kuti akhale ndi umboni wonse. +Sindidalandire lipoti lililonse lokhudza nkhani za ku Zombazi. Ndifufuze kaye kuti zidayenda bwanji, adatero Chiumia. +Koma mkulu wa bungwe lopereka upangiri ndi thandizo pa maufulu a anthu la Centre for Human Rights, Education, Advice and Assistance(CHREAA), Victor Mhango, adati mchira wanyani udakhota pachiyambi pomwe ena mwa apolisiwa ankalembedwa ntchito. +Mhango adati ambiri adalowa ntchitoyi chifukwa chodziwana ndi ena mwa andale ndipo alibe chidwi chenicheni chogwira ntchito yachitetezo koma kudzilemeretsa. +Iye adati enanso mwa apolisiwa amaona ngati lamulo silingawakhudze ndipo akhoza kupalamula ngakhale kuzunza anthu umo angathere popanda kulandira zilango zamtundu uliwonse. +Akavala yunifolomu ija ndi kutenga unyolo mmanja amaona ngati basi palibe angawakhudze, adatero Mhango. +Iye adati nzamanyazi kuti ena mwa apolisiwa akumafika pamlingo wochita nawo za umbava ndi umbanda mmalo moteteza anthu. +Agulitsa chimanga kudziko la tanzania Pomwe boma lili pakalikiriki kuitanitsa chimanga kuchokera kunja pofuna kupulumutsa Amalawi ku galu wakuda yemwe wadutsa madera ambiri mdziko muno kaamba ka kuchepa kwa mvula chaka chatha, zamveka kuti Amalawi ena agundika kugulitsa chimanga chawo kudziko la Tanzania. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Themba la Mathemba (Paramount Chief) Chikulamayembe ya mboma la Rumphi yauza Tamvani, kuti alimi ambiri mdera lake agulitsa chimanga chawo mozemba kumavenda ochokera mdziko la Tanzania mmalo mogulitsa kumisika ya Admarc. +Iye adati izi zikuchitika ngakhale ena mwa anthu ake ali pachiopsezo chachikulu chokulukutika ndi njala. +Chikulamayembe: Kulankhula ndiye tikulankhula koma ena samamva Chimanga chidachitako bwino pangono chigawo cha kumpoto,kuphatikizapo boma la Rumphi, koma makomo ambiri avutikabe ndi njala. Izi zili chomwechi chifukwa chimanga chambiri chalowa mdziko la Tanzania, adatero Chikulamayembe. +Mfumuyi idati kumbali yake ikuyesetsa kuchititsa misonkhano kuuza anthu za kuipa kogulitsa chimanga kunja pomwe mdziko muno muli njala yadzaoneni. +Ambiri akumvetsa, koma ena amakopekabe ndi mitengo yokwera yomwe mavenda akunjawa amapereka powagula poyerekeza ndi ya Admarc koma amaiwala kuti nthawi yanjala adzagulanso chimanga chomwecho kwa mavenda omwewo pamtengo wokwera kwambiri, adatero Chikulamayembe. +Iye adapempha boma kuti lichitepo kanthu pokhwimitsa chitetezo mmalire a dziko lino ndi maiko oyandikana nawo kuti chimanga chosowachi chisamatuluke chisawawa. +Pakalipano, boma la Malawi layambapo kuitanitsa chimanga kuchokera kumaiko ena monga ku Brazil, Ukraine, Mexico ndipo china chayamba kale kulowa mdziko muno kuchokera ku Zambia. +Anthu oposa 6.5 miliyoni mdziko muno alibiretu chakudya moti akufunika thandizo mwachangu, malinga ndi lipoti la Malawi Vulnerability Assessment Committee (Mvac). +Powunikira izi, ndondomeko ya zachuma ya dziko lino idaika padera ndalama zokwana K35 biliyoni zogulira chimanga mdziko muno komanso kumaiko akunja chokwana pafupifupi matani 1 miliyoni choti anthu adzadye njala ikafika posauzana. +Chanda Kasolo, mmodzi mwa akuluakulu omwe ali mukomiti ya pulezidenti wa dziko la Zambia yoyanganira chimanga ndi zina zotere lotchedwa Presidential Multi-Agency Taskforce on Maize, Maize Products and Food Security, adatsimikiza kuti dziko lino lidaitanitsadi chimanga chopitirira matani 500 000, ndipo matani 150 000, adatumizidwa kale sabata zitatu zapitazo. +Iye adati chimangachi chikugulidwa pamtengo wa pafupifupi $15 (MK11 250) pathumba la makilogalamu 50 lililonse. +Koma pomwe ena ku Rumphi akugulitsa chimanga kwa mavenda a ku Tanzania, Lachinayi sabata yatha boma la Zambia lidalanda matani 90 a chimanga kudzanso matani 30 a ufa omwe ena amafuna kulowetsa mdziko muno mozembetsa. Mu April dzikolo lidagwiranso galimoto zikuluzikulu 28 zitanyamula chimanga chomwe amafuna kulowa nacho mdziko muno mosatsata ndondomeko. +Kasolo adati Amalawi asabwekere chimanga cholowa mdziko muno mozembetsedwa chifukwa chikumagulitsidwa pamtengo wodula kwambiri. +Akumachigula pamtengo wa K80 ya Zambia (yomwe ndi pafupifupi K5 678 ya Malawi) ndipo akuchigulitsa mokwera kwambiri kwa Amalawi mboma la Mchinji, adatero Kasolo. +Iye adati boma la Zambialo ndi lokhumudwa ndi mchitidwewu chifukwa ukulowetsa pansi chuma cha maiko awiriwa. +Pokambapo za mmene zilili mdziko muno, Symon Vuwa Kaunda, mmodzi wa alangizi a pulezidenti wa dziko lino, adauza atolankhani kuti chigawo chakumpoto, makamaka boma la Mzimba, kuli chimanga chambiri zedi chomwe bungwe logula ndi kugulitsa mbewu kwa alimi la Agriculture Development and Marketing Corporation (Admarc) silitha kugula chonse. +Koma Kaunda adangoti kakasi, kukaninka kuyankha atamufunsidwa kuti nchifukwa chiyani boma likulimbana ndi chimanga chakunja pomwe likukanika kugula chimanga chamnanu chomwe iye akuti chilipo mboma la Mzimba. +Ndipo zidali zamanyazi pomwe atolankhani adafika ku depoti ya Admarc mumzinda wa Mzuzu komwe adapezako matani 2 800 okha. Malowa amadzadza ndi matani 10 000. +Kafukufuku wa Mvac adati boma la Mzimba ndi limodzi mwa maboma omwe akhudzidwe ndi njala mwa anthu 12 pa 100 alionse pomwe anthu 16 pa 100 alionse avutika ndi njala mboma la Rumphi. +Koma mavuto aakulu ali mmaboma a Nsanje ndi Chikwawa komwe, malinga ndi lipoti la Mvac, pafupifupi anthu 90 pa 100 alionse alibiretu chakudya moti ngati slandira thandizo la chakudya msanga ambiri afa ndi njala. +Maboma ena komwe galu wakuda wavuta kwambiri ndi Balaka, Blantyre, Zomba, Machinga, Mangochi ndi Thyolo mchigawo cha kummwera. +Chokhumudwitsa kwambiri nchakuti mbewu zina monga chinangwa, mbatata ya kholowa ndi kachewere kudzanso mapira, zomwe anthu amapulumukirapo chimanga chikalephereka, nazonso sizidachite bwino kaamba ka chilala. +Mzungu wolemba dikishonale ya Chichewa Dikishonale kapena kuti buku lotanthauzira mawu ndi imathandiza anthu kupeza matanthauzo a mawu omwe akuwavuta kuti amvetsetse zomwe nkhani ikukamba. Nthawi zina pamakhala dikishonale yotanthauzira mawu a chilankhulo china kupita mchilankhulo china. Mmodzi mwa anthu omwe dikishonale yotanthauzira Chichewa mChingerezi ndi mzungu wa ku Netherlands Steven Paas yemwe pano ali ndi zaka 74 zakubadwa ndipo wayenda ndi kuzungulira kwambiri pakati pa Achewa. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere: Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Paas: Ndinkavutika pophunzira Chichewa Ndiuzeni mbiri yanu. +Dzina langa lonse ndi Steven Paas ndipo ndidabadwa mu 1942 kwathu ku Netherlands. Ndimagwira ntchito za Mulungu imene ndidadzapezekera ku Malawi kuno. +Ndinu mzungu, ganizo lotanthauzira mawu a mChichewa lidabwera bwanji? Chidwi chophunzira Chichewa chidakula kwambiri mmbuyomu. Pophunzira chilankhulochi ndinkakumana ndi zokhoma chifukwa kudali kovuta kumvetsetsa mawu ena. Ichi chidali chipsinjo chachikulu zedi moti zidandipangitsa kuyamba kulemba mawu ndi matanthauzo ake ndikawamva koyamba. +Mawuwa munkawamva kuti? Monga ndanena kale, munthune ndine mtumuki wa Mulungu ndiye ndimakumana ndi anthu osiyanasiyana omwe amakhala ndi mawu osiyanasiyana. Kupatula apo, ndimakonda kuyenda mmadera kufufuza zomwe anthu amachita ndiye zina mwa zomwe zili mbukhuli ndi zochitika mmadera makamaka ozungulira malo a Achewa omwe ndimacheza nawowo. +Sipangalephere mavuto, mudakumanapo ndi mavuto otani? Monga mudziwa kuti nthawi zambiri anthu amakhala otchingira kwambiri makamaka pa zokhudza miyambo yawo kotero nthawi zina pofufuza, anthu ena amatha kuona ngati ndikuwafwala ndiye poteropo sizimayenda bwino mpakana ena omvetsetsa alowererepo ndi kundithandiza. +Makamaka bukuli lidalembedwa motani? Ndimalemba liwu la Chichewa nkulitanthauzira kenakonso lomwelo nkulilemba mChingerezi nkulitanthauziranso kuti onse Achewa ndi Azungu apindule nalo komanso kwa ena, akhoza kuphunzira Chingerezi kapena Chichewa mosavuta poligwiritsa ntchito. +Zidakukomerani bwanji kukhazikitsa bukhu lolumikiza zilankhulo ziwiri? Ndiyambira pa Malembo Oyera omwe amapezeka pa Genesesi 11 pomwe anthu adaganiza zomanga nsanja yokafika kumwamba ndipo Mulungu adawasokoneza ndi zilankhulo zosiyanasiyana kuti pulani yawo isatheke. Pamenepa pali phunziro lakuli ndipo nkofunika ndithu kuti anthu ngakhale ali a zilankhulo zosiyanasiyana, pakhale njira yoti azimvana mosavuta. Mukadzalimvetsetsa buku, mudzaona kuti mposavuta munthu kumvetsetsa nkhani mChichewa kapena mChingerezi poligwiritsa ntchito. Apa ndiye kuti anthu azilankhulo ziwirizi athandizika. +Msonda: Tsamba loyoyoka mu PP? Nthawi yomwe anthu akuchoka mchipani cha Peoples Party (PP) chitangogwa mboma, mneneri wa chipanichi, Ken Msonda, yemwe ali ndi lilime lakuthwa komanso amayankhula mokhadzula, amawayerekeza anzawowo ngati masamba ouma amenene akuyoyoka mmitengo nthawi ya chilimwe. +Lero zagwa pamphuno. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Wachoka mu PP: Msonda Kodi pano Msonda nditsamba louma limene lathothoka mchipani chakale cholamula kuti zichitire ubwino chipanichi? Wogwirizira utsogoleri wa PP, Uladi Mussa akuti Msonda, ngati wina aliyense, ali ndi ufulu wochoka mu chipanichi. +Msonda akunenetsa kuti iye ndi katakwe pandale ndipo kuchoka kwake mchipanichi sikutanthauza kuti ukatakwe wake pandale watha, ayi, koma akumvera zimene Mulungu wake akumuyankhula. +Iye dzana Lachinayi adalonjedza kuti auza mtundu wa Malawi zifukwa zochokera mchipanichi ndi zomwe akulingalira kuchita pamoyo wake mtsogolomu pamsonkhano wa atolankhani mumzinda wa Blantyre, koma dzulo, iye adasintha thabwa ndi kuuza atolankhani kuti msonkhanowu walepheleka atamvera malangizo a mbusa wake. +Abusa anga andiuza kuti ndisapangitse msonkhano wa atolankhaniwu. Akuti ndidekhe kaye mpakana nthawi yoyenerera yokhazikitsidwa ndi Mulungu itakwana. +Ndikupempha anthu kuti andimvetsetse. Monga mmene ndanenera kale, ndikufuna kuzamisa moyo wanga wa uzimu komanso kukhala ndi nthawi yokwanira ndi banja langa, Msonda adatero. +Mkuluyu adati adayankhulana ndi mtsogoleri wa chipani cha PP, Joyce Bandaamene ali kunja kwa dziko lino komwe akhala chigonjereni pazisankho za mu 2014za kuchoka kwake. +Msonda adati Banda adamupempha kuti asachoke msanga kufikira iyo atabwerera ku Malawi, koma idati izi sizikadagwirizana ndi chikonzero chake chopempha Mulungu kuti amutsogolere pa za tsogolo lake mundale komanso muuzimu. +Iye adati zomwe amayankhulira anzake powayerekeza ngati masamba ouma amene akuthothoka mumtengo nthawi ya chilimwe zidali gawo la ntchito yake potumikira chipani. +Ngati mmeneri wa chipani, ndimayenera kuyankhulira chipani komanso kupereka chithunzithunzi chabwino cha chipanichi kumtundu wa Malawi. Koma izi sizikusonyeza kuti ine ndi tsamba louma lomwe latha ntchito. +Poti ndanena kuti ndikufuna ndizame muuzimu kaye, za ine akambe ndi anthu. Ndale ndazisiya kale apo, koma mtsogolomu mundiona ndikuzapanga nawo mpikisano pachisankho cha aphungu a ku Nyumba ya Malamulo mu 2019, Msonda adatero. +Mkuluyu, yemwe wakhala akusintha zipani komaso amadziwika kwambiri ndi dzina loti Foot Soldier, akuti panthawi yoyenera adzauza anthu dongosolo limene akupempha Mulungu kuti amukonzere. +Msonda, yemwe lilime lake lamuikako mmavuto potengeredwa kukhoti atamemeza anthu kuti azipha anthu amene amagonana amuna okhaokha kapena akazi okhaokha, adalowa mu chipani cha PP mu January 2012, chipanichi chisanalowe mboma koma mayi Banda ali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino malemu Bingu Wa Mutharika. +Iye adasankhidwa kukhala mneneri wa PP ndipo udindowu udapitirira chipani cha PP chitalowa mboma potsatira imfa ya Bingu wa Mutharika. +Msonda, yemwe adakhalakonso wothandizira mmeneri mchipani cha UDF asadalowe PP, wakhala akusowetsa mmtendere chipani cholamula ndi kuyankhula kwake kokhadzula, ndipo kumayambiriro a chaka chino, adauzapo mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika kuti atule pansi udindo wake kaamba koti alephera kukonza vuto la zachuma ndi zina. +Izi anayankhula kumsonkhano wa anthu onse okhuzidwa wa Public Affairs Committee (PAC)mu mzinda wa Blantyre, ndipo kuyankhula uku kudakwiyitsa nduna zambiri zomwe zinkatenga nawo gawo kumsonkhanowu. +Chipani cha PP chakhala chikutaya atsogoleri ake ofunikira kwambiri kuphatizapo Sidik Mia, yemwe adatula pansi udindo wake ngati pulezidenti wothandizira mchigawo cha kummwera chisankho za 2014 chitatsala pangono. +Gondwe azaza pamsonkhano Nduna ya za chuma Goodal Gondwe Lolemba idazaza pamwambo wosayinirana pangano la ngongole ndi banki ya zachitukuko mu Africa ya African Development Bank (AfDB) itazindikira kuti akuluakulu a kuundunawu sadabweretse mapepala osayinira panganolo. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndunayi imayembekezera kusayinira pangano la ndalama zokwana US$22 miliyoni (pafupifupi K16 biliyoni) mmalo mwa boma ndi oyimilira bankiyi Andrew Mwaba ku likulu la undunawu ku Lilongwe. +Adakwiya: Gondwe Cholinga cha ndalamazi nkupititsira ntchito za ulimi patsogolo ndi kutukulira achinyamata paulimi. +Gondwe adakhumudwa ndi kulephera kwa akuluakulu a kuundunawu kuzindikira kuti mwambowo udayamba palibe mapepala ofunikirawo ndipo adadula mkamwa oyendetsa mwambowo Alfred Kutengule kuti za mapepalawo zilongosoke. +Zitheka bwanji kusayinirana pangano popanda mapepala ofunikira? Tisayina pati? Mapepala ali kuti apa? Adafusa Gondwe. +Ndunayi itangolankhula izi, kudali yakaliyakali akuluakuliwo kuthamangathamanga mmawofesi kusaka mapepalawo kuti mwambo upitilire ndipo pomwe mapepalawo amapezeka, makina achinkuza mawu omwe amagwiritsidwa ntchito pa mwambowo adasiya kutulutsa mawu. +Apolisi akuthetsa milandu ku Nthalire Apolisi ena ku Nthalire mboma la Chitipa akuweruza ndi kuthetsa milandu osaipititsa kubwalo la milandu. +Izi zidadziwika sabata yapitayi pomwe bungwe la National Initiative for civic Education (Nice) lidachititsa msokhano mderalo. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Aka si koyamba kuti nkhani zotere ziphulike papolisipo. Mmodzi mwa akuluakulu a bungwe la Catholic Commission for Justice and Peace (CCJP) mbomalo, John Moyo, atalandira malipotiwo adaitanitsa mkulu wapolisiyo mwezi wa June chaka chatha. +Tidawaitanitsa kumsonkhano umene onse okhudzidwa akadakhalako koma poyamba adati ndiwotangwanika. Tidakonza tsiku lina ndipo tidachita kukawatenga. Adavomera kuti zimalakwika ndipo adati izi zitha, adatero Moyo. +Koma mkulu wa polisi ya Nthalire Ben Mwaliwa adati pamsonkhano watsopanowu iyeyo padalibepo. +Ine ndikudziwa za msonkhano wa chaka chatha omwe lidakonza ndi bungwe la CCJP. Pamsonkhanowu tidalonjeza kuthetsa mchitidwewu. Mbuyomu madandaulo amenewo adalipo koma zoti pano kukumalandiridwa ndalama ndinamapo, adatero Mwaliwa. +Atafunsidwa ngati akumatumiza milandu ku bwalo la milandu, iye adavomera kuti polisi ya Nthalire ikumatumiza milandu kubwalo la milanduyi. +Malinga ndi ofisala wa bungweli mboma la Chitipa, Amos Ngoma, akomiti za chitukuko komanso anthu okhudzidwa adatambasula pamsonkhano wapadera sabata yatha kuti milandu ikumathera kupolisi komwe apolisiwa akumapatsidwa ndalama potengera ndi kukula kwa mlandu. +Apa tidapempha oweruza milandu mderali kuti azipita kupolisi tsiku ndi tsiku kukatenga malipoti a anthu otsekeredwa mchitokosicho kuti aziunika omwe angapatsidwe belo pasanathe maola 48, adatero Ngoma. +Kutulutsidwa kwa anthu asanatengeredwe kukhoti kwachititsa kuti bwalo la majisitileti ku Nthalire lisamalandire milandu zomwe zikupereka mafunso kwa ena mwa anthu ogwira ntchito pabwalopo chifukwa Nthalire ndi tauni yaikulundithu, imenenso ili mmalire a dziko lino ndi la Zambia ndipo kupalamula nkwakukulu. +Malinga ndi ena mwa ogwira ntchito pabwalopo omwe sadafune kutchulidwa maina poopa kuchitidwa chipongwe, bwaloli limayembekezera kumazenga milandu itatu kapena inayi pa tsiku. +Koma padakalipano palibe ngakhale mlandu ndi umodzi omwe ukutumizidwa kubwaloli. +Tikakafufuza kupolisi timapeza kuti anthu ali mchitokosi ndithu; koma milanduyi ikumathera konko, adatero anthuwo. +Pomwe CCJP adachititsa msonkhano mu June, mfumu Chipuwe idati mwana wake wamwamuna adauzidwa kuti apereke K60 000 kuti akatenge njinga yake yomwe idali mmanja mwa apolisi kaamba koti adachita nayo ngozi. +Ndipo nawo a bwalo la milandu pa nthawiyo adanenetsa kuti iwo adadziwa kuti china chake si chili bwino kupolisi chifukwa samalandira milandu ngati momwe zilili pano. +Mneneri wa apolisi mchigawo cha kumpoto, Peter Kalaya, adati ngakhale ofesi ya polisi ya Chitipa ikumamvera za nkhaniyi mmisonkhano ndipo palibe wapitako kukawadandaulira za nkhaniyi. +Pena pake tikudziwa kuti anthuwa amaopa chifukwa nkhani za katangale zimakhudza anthu awiri. Nawonso amaopa kuti ziwakhudza, adatero Kalaya. +Shuga apezeka posachedwaIllovo Mkulu wa kampani yopanga shuga ya Illovo Malawi Mark Bainbridge wati kampaniyo iyesetsa kuti shuga azipezeka chaka chonse osati kumasowa momwe zakhalira sabata zingapo zapitazi. +Bainbridge adanena izi Lachitatu pomwe nduna ya zokopa alendo ndi malonda Joseph Mwanamvekha adayendera kampaniyo kuti akamvetsetse za gwero la kusowa kwa shugayo. Kusowa kwa shuga kudachititsa kuti ogulitsa akweze kuchoka pa K750 kufika pakati pa K950 ndi K1 200. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ogwira ntchito ku Illovo pakalikiliki kupanga shuga Malinga ndi Bainbridge, chaka chino kampaniyo inagulitsa shuga olemera matani 244 000, pomwe dziko lino limalira matani 160 000 ndipo anadabwa kuti shugayo akusowa bwanji. +Tinali ndi shuga wokwanira chaka chino ngakhale mvula siyinagwe bwino nthawi yomwe timabzala nzimbe. Ogulitsa ena amagula shuga wochuluka nkumusunga zomwe zimadzetsa mavuto ngati awa, adatero iye. +Iye adati padakalipano, kampaniyo ikuyesetsa kuti iwonjezere shuga amene imapanga kuti azikwanira chaka chonse. +Mwanamvekha adati ndi wokondwa chifukwa kampaniyo yalonjeza kuti izipanga matani 650 a shuga patsiku, pomwe dziko lino limalira matani 411 patsiku. +Tazindikira kuti pali shuga wochepa pamsika, zimene zachititsa kuti mtengo ukwere. Kwa amene akukweza shuga mopweteka Amalawi, malamulo agwirapo ntchito. Tili ndi chiyembekezo kuti Illovo ikwaniritsa lonjezo lake kuti shuga ayambe kupezeka, adatero Mwanamvekha. +Pomwe Amalawi akudikira shugayo kuti ayambe kupezeka, Amalawi amene tidacheza nawo anadandaula ndi kusowa kwa shugako, ponena kuti izi zikuchititsa moyo kuthina. +Mmodzi mwa Amalawiwo, Joana Chimphamba wa kwa Senti ku Lilongwe, adati abizinesi ena kumeneko akumaphwatula paketi ya kilogalamu imodzi ndi kuigawa pawiri. Gawo lililonse akuligulitsa K600 kapena K650. +Izi zikutanthauza kuti yomwe timagula K780 pa paketi tikugula K1 200 kapena K1 250. Nanga akapitirira kusowa shugayu, zitithera bwanji? adadabwa iye. +Chimvano Moyo wa ku Area 25 wati poyamba sadakhulupilire atatuma mwana kukagula shuga Lamulungu lapitali ndipo pobwera adamuuza kuti adagula pa mtengo wa K970 chikhalirecho, amagula pamtengo wa K780. +Iye wati atapita kukatsimikiza kumsika, adapeza kuti magolosale ambiri alibe shuga ndipo pomwe adamupezapo adamutsimikizira kuti shuga akusowa ndipo akapezeka akukhala okwera mtengo. +Mmodzi mwa anyamata ogwira ntchito mushopu yaikulu ya Spar mumzinda wa Lilongwe adati patenga nthawi shopuyi isanalandire shuga kuchokera ku Illovo. +Iye adati anthu ambiri akhala akubwerera mushopuyi akafuna shugayo ngakhale kuti eni ake adapereka kale oda ya katunduyu koma sadanene kuti shugayo samabwera chifukwa chiyani. +Ndipo mumzinda wa Blantyre, anthu ochuluka amakhamukira kusitolo zosiyanasiyana monga Shoprite kumene kumakhala miyandamiyanda ya anthu pamzere kufuna kugula shuga akapezeka. +Davie Chilikumwendo wa ku Namiyango mu mzinda wa Blantyre adati wasiya kumwa tiyi chifukwa ndalama ya shuga siyikukwanira. +Shuga yemwe akupezeka akugulitsidwa pamtengo wokwera. Padakalipano tizigwiritsa mchere mphala ndipo tiyi adzamwedwa shuga akayamba kugulitsidwa pa mtengo woyenera, adatero Chilikumwendo. +Nawo ochita malonda mumzindawu ati kusowa kwa shuga kukusokoneza bizinezi chifukwa amadalira yemweyi popanga phindu lochuluka. Mmodzi mwa iwo, Clement Chafoteza wa ku Chilobwe, adati shuga wochepa yemwe akupezeka akugulidwa modula ndipo anthu wamba akukanika kuagula. +ACB idayamba kale kufufuza Chaponda Nthambi yofufuza za ziphuphu ya Anti-corruption Bureau (ACB) yati idayamba kale kufufuza nkhani ya momwe bungwe la Admarc lidagulira chimanga mdziko la Zambia. +Mkulu wa ACB Lukas Kondowe adanena izi Lachitatu, patangotha masiku angapo kuchokera pomwe komiti imene lidasankhidwa ndi mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika kuti lifufuze ngati nduna ya za malimidwe George Chaponda ikukhudzidwa pankhani yoti bungwe la Admarc lidasokoneza zina pogula chimangacho kupyolera mu kampani ya Kaloswe Courier and Commuter Services ya ku Zambia. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Afufuzidwe: Chaponda Mwa zina, gululo, limene limatsogoleledwa ndi Anastazia Msosa, lidapempha Mutharika kuti ACB ifufuze momwe nkhaniyi idayendera. Koma Kondowe adati adayamba kale izi. +Tidayamba kale ngakhale mtsogoleri wa dziko lino asadakhazikitsenso komiti yapadera. Choncho tingopitiriza basi, adatero Kondowe. +Polankhula ndi mtolankhani wathu, Kondowe adati adangomva pawailesi za kupsa kwa ofesi ya Chaponda Lachiwiri ndipo adati akudikira lipoti la momwe maofesi a Chaponda ndi akuluakulu ena adapsera. +Sitikudziwa ngati zomwe tikadafuna mkafukufuku wathu kumeneko, zaonongeka nawo ndi motowo, adatero Kondowe. +Motowo udaononga ofesi ya nduna Malinga ndi mkulu wa apolisi Lexten Kachama amene adafika pamalo a ngoziyo adati apolisi akufufuzabe chidayambitsa motowo cha mma 11 koloko mmawa. +Motowo udadzetsa mtsutso pakati pa Amalawi pamene ena ankati udabuka pofuna kusokoneza umboni pomwe ena ankati ndi ngozi chabe. +Polankhulapo, mmodzi wa a mabungwe omwe si a boma omwe adakatenga chiletso mwezi watha kuti ndunayi ayiimitse kaye pantchito mpaka kafukufukuyu atachitika Moses Mkandawire adati kuyaka kwa ofesiku kukufunika kufufuzidwanso mwapadera. +Mkandawire, yemwe ndi mkulu wa bungwe loona za kakhalidwe ka anthu ya Church and Society mu sinodi ya Livingstonia, adati pakadalipano ndi zovuta kuloza zala munthu kuti ndiye wayatsa motowo. +Sitingaloze zala munthu kuti ndiye wayatsa moto; koma chofunika ndi kafukufuku wina kuti ofesiyi idayaka bwanji panthawi ngati ino pomwe ili mkamwamkamwa mwa anthu? Bwanji siyidayake ofesi ya zofalitsa nkhani kapena ofesi ina? Kodi tingati izi zangochitika? adadabwa Mkandawire. +Iye adati chopweteka kwambiri nchoti failo ndi uthenga wambiri waboma waonongeka ndi motowo zomwe zingasokoneze ntchito za boma zomwe zimayenera kupitilizidwa ndi anthu osiyanasiyana. +Izitu nzopweteketsa ana athu chifukwa tawaonongera uthenga wofunika womwe akadadzaugwiritsa ntchito mtsogolo muno kaamba koti zinthu zathu zambiri sizili pa intaneti n gati maiko aanzathu, adatero Mkandawire. +Komabe Mkandawire adayamikira Mutharika pokhazikitsa komiti yapaderayo komanso adayamikira zotsatira za kafukufukuyo ati popeza adangotsimikizira zomwe mabungwe omwe siaboma akhala akunena kuti Chaponda ngofunika kufufuzidwa bwino. +Malinga ndi lipotili Chaponda akuyenera kufufuzidwa pa momwe adalowerererapo kuti kampani ya Transglobe ikhale nawo mgulu logulitsa boma chimanga. +Pali kukaikitsa pa njira yomwe kampani ya Transglobe idapezera chiphaso chotumizira chimanga kuchokera mdziko la Zambia kubweretsa kuno, choncho Chaponda akuyenera kufufuzidwa mbali yomwe adatengapo, idatero lipotilo. +Lipotili lidatinso bungwe la ku Zambia la Zambia Cooperative Federation lomwe adali pamgwirizano ndi bungwe Admarc loperekera chimanga chokwana matani 100 000, lidangoperekapo matani 4 000 okha. +Padakalipano komiti yapadera ku Nyumba ya Malamulo, Lachitatu limayembekezera kutulutsa zotsatira zake. +Poyankha mafunso a komitiyo sabata yatha, Chaponda adati nkhaniyo siyimamukhudza kwambiri chifukwa gawo lake lidali kukambirana ndi nduna ya malimidwe ku Zambia kuti boma la Malawi likufuna chimanga. Za ndondomeko yogulira chimangacho, iye adatero, idali mmanja mwa Admarc. +Dziko lathu lidali pamoto wa njala. Ngati nyumba ikupsa, mukhonza kuthyola zitseko ndi mawindo kuti mupulumutse mwana amene angafere momwemo. Ndondomeko zina sizinatsatidwe chifukwa tidali pampishupishu, Chaponda adatero. +Boma lifalitsa lipoti la zotaya mimba Boma latulutsa lipoti la zotsatira za kafukufuku wa wokhudza za Malamulo ochotsa mimba yemwe bungwe lapadera lofufuza za malamulowo lidachita mu 2015. +Lipotilo lidaperekanso maganizo ake kuti Malamulo okhudza kuchotsa mimba asinthidwe kuti azilola amayi amene atenga pakati atagwiriridwa, ngati mayi atenga mimba atagonana ndi mbale wake, komanso ngati mimba ingadzetse paumoyo ndi maganizo a mzimayi. Padakalipano Malamulo a dziko lino amangolola kuchotsa mimba ngati iyika pachiopsezo moyo wa mayiyo. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Chavula kuonetsa lipotilo Wachiwiri kwa mkulu wa zosintha Malamulo ku Law Commission, Edda Chavula, unduna wa zamalamulo udzatulutsa bilo yokhudza msinthowo ndipo aphungu a kawakambirana. +Takondwera kwambiri chifukwa boma tsopano lavomereza lipotilo, limene a Law Commission adachita atatumidwa ndi Unduna wa Zaumoyo, adatero Chavula. +Mwa zina, lipotilo lidapeza kuti kuli imfa zochuluka za amayi ofuna kuchotsa pakati mobisa amene amagwiritsa zinthu zina monga zitsamba, mitengo, mawaya ndi zina zotere. Amayiwo akapita kuchipatala, achipatala amakachotsa zotsalira za khanda lotaidwalo koma ena amapita kuchipatala mochedwa, zimene zimadzetsa imfa. +Mkulu wa mabungwe ounikira kuti amayi asamachotse pakati moika miyoyo yawo pachiswe la Coalition for the Prevention of Unsafe Abortions (Copua) Simon Sikwese adati akondwa ndi kuvomereza kwa lipotilo. +Takondwa ndipo tikuyembekeza kuti aphungu adzakambirana za lamuloli mtsogolomu. Malamulo amene alipo pano amaika pachiopsezo miyoyo ya amayi ndi asungwana, adatero Sikwese. +Malinga ndi kadaulo wa zaumoyo wa amayi Dr Chisale Mhango wa ku College of Medicine, kafukufuku adasonyeza kuti mimba 141 000 zidachotsedwa mu 2015. +Ngati madotolo komanso a zakafukufuku, tidapeza kuti chipembedzo sichilepheretsa amayi kuchotsa mimba. Ngakhale Malamulo akhwime chotani, amayi amachotsabe mimba. Izi zimangochititsa kuti achotse mimbazo modzivulaza, adatero Mhango. +2017 yatilandira ndi zigumula Pangotha sabata chilowereni chaka cha 2017, koma malipoti a ngozi zakudza ndi mvula mmaboma osiyanasiyana atopetsa kale. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Nyumba, sukulu, misewu, katundu ndi zakudya za anthu ena zaonongeka ndipo Amalawi ena ali pamavuto kaamba ka ngozizo. +Lachitatu lapitali, nyumba 32 zidasasuka kudzanso zipupa zina kugwa kaamba ka mvula ya mphepo ya mkuntho yomwe idagwa kwa mfumu yaikulu Mkukula mboma la Dowa komwe idaononga katundu ndi chakudya. +Mlatho wa pa Jalawe ku Rumphi udaguvukira mvula itakokolola zoulimbitsa Agulupu aakulu a Mengwe omwe dera lawo lidakhudzidwa kwambiri adati mvula ndi mphepozo zidayamba mma 3 Koloko masana a tsikulo ndipo mmudzimo mudali kokakoka anthu kusowa kolowera ndi pogwira. +Chakudya chathu monga ufa, pogona ndi zofunda komanso katundu wina ofunika zidaonongeka pangoziyo moti ndi mwayi kuti palibe yemwe adavulala, adatero Mengwe. +Mkulu wapolisi mbomalo Felix Phiri adakafotokozera ofesi ya DC momwe zinthu zilili apolisi atakayendera madera okhudzidwawo kuti athandizane zochita. +Lachitatu lomwelo, anthu 7 adavulala pamalo okwerera basi a Mibawa mumzinda wa Blantyre mvula yamphamvu itazula chimtengo chomwe chidali pafupi ndi malowo nkuwugwetsera pa maminibasi 7. +Lachiwiri, mvula ina ya mphamvu idakokolola mlatho wa Jalawe omwe umalumikiza maboma a Rumphi ndi Karonga pa msewu wa M1. +Malingana ndi DC wa mboma la Rumphi Lusizi Nhlane, mvula yamphamvu idagwa usiku wa Lachiwiri zomwe zidapangitsa kuti madzi aziyenda mwamphamvu mpakana kufowola mizati ya mlathowo omwe udakokoloka. +Ngozi zina zokhudzana ndi mvula yamkuntho zidachitika tsiku loyembekeza kulandira chaka cha tsopano pa 31 December, 2016 mdera la mfumu yaikulu Nanseta mboma la Thyolo komwe nyumba 114 zidaonongeka. +Kauni yemwe khonsolo ya boma la Thyolo adachita wasonyeza kuti chiyambire mvula ya chaka chino, nyumba 1 000 ndizo zakhudzidwa ndipo izi zapangitsa kuti mavuto a malo okhalapo akule mbomali. +Pa 31 December, 2016 pomwepo, nyumba 96 zidaonongeka ndi mvula yamkuntho yomwe idagwa mboma la Karonga ndipo a komiti ya zachitetezo ya District Civil Protection (DCPC) adati izi zidafikitsa chiwerengero cha nyumba zokhudzidwa pa 424 mbomali. +Komitiyo idati midzi ya Mwamutawali, Mponera ndi Mwandovi ndi ina mwa midzi yomwe yakhudzidwa ndi mvula zolusazi mbomali ndipo zina mwa zomwe zaonongekeratu ndi sukulu ya pulaimale ya Chisumbu ndi msika wa Jetty. +Nthambi yoona zanyengo mdziko muno idalengeza kumayambiriro a Mvula kuti chaka chino dziko lino liyembekezere mvula yamkuntho chifukwa cha mphepo ya La Nina yomwe nthawi zambiri imabweretsa mvula yamtunduwu. +Pankhaniyi, mneneri wa nthambi yoona ngozi za dzidzidzi Jeremiah Mphande adati ndilokonzeka kulimbana ndi zotsatira za Mvula ya mtunduwu itati yabwera chifukwa ilo mothandizana ndi maiko ena komanso mabungwe adakhazikitsa kale ndondomeko zoyenera. +Avulaza shehe akuitanira mapemphero Nthawi ikamathamangira 5 koloko mmawa, anthu achipembedzo cha Chisilamu amadzutsidwa kuti akachite mapemphero kumzikiti pamene shehe kapena mwazini (muezzin) amakhala akukuwa. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Koma zachitika ku Nkhotakota si ndizo komwe anthu achiwembu avulaza shehe amene amaitanira mapempherowo. +Ali mu ululu: Shehe Ainani kulandira chithandizo mchipatala Mneneri wa polisi ya Nkhotakota, Williams Kaponda, wati izi zidachitika mmawa wa Lachitatu lapitali ndipo sheheyu adamugoneka mchipatala cha Nkhotakota. +Kaponda adati sheheyu dzina lake ndi Namandwa Ainani, wa zaka 57, amene akuchokera mmudzi mwa Malenga kwa Senior Chief Malengachanzi mbomalo. +Ainani adadzuka mmawa pamene amamemeza anthu achipembedzo cha Chisilamu kuti adzuke akapemphere kumzikiti wa Malenga. +Chu uyu mpaka liti? Njala yayamba kuluma mmadera ena koma ngakhale zili chonchi, boma lati anthu asayembekezere kuti misika ya Admarc itsegulidwa msanga kaamba koti ntchito yogula chimanga ikadali mkati. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Nduna ya zamalimidwe, mthirira ndi chitukuko cha madzi George Chaponda idauza nyuzipepala ya The Nation posachedwapa kuti boma silingatsegule misika lisadamalize kugula poopa kuti mavenda angagule chimanga ku Admarc nkukagulitsanso ku Admarc komweko. +Kuti titsegule msika pomwe tikugula, anthu adzagula nkutigulitsanso chifukwa Admarc imagulitsa pamtengo otsika. Zinthu zikalongosoka, tidzalengeza za tsiku lotsegulira msika wa Admarc, adatero Chaponda. +Gondwe: Mtima pansi Pakalipano, anthu ambiri, makamaka mboma la Nsanje kuchigwa cha Shire komwe njala yafika kale povuta, akupulumukira mbatata ndi zomera mumtsinje wa Shire zotchedwa nyika zomwe mmiyezi ikudzayi ziyambe kusowa malingana nkuti mbewu ngati izi zimapezeka panyengo yochepa. +Koma njalayi sikuti yakhudza madera akumidzi okha ayi, koma ngakhale mmatauni ndi mizinda ina mdziko muno. +Maria Kalowekamo, yemwe ndi kholo la ana anayi koma mwamuna wake adamwalira ndipo akukhala kwa Chinsapo mumzinda wa Lilongwe, adati nkhawa yake ili pakuti mbewu ngati mbatata zikayamba kusowa adzavutika kwambiri kusamalira ana akewo. +Panopa zikuoneka ngati zopepukirako pangono chifukwa zakudya zina monga mbatata zikadapezeka mmisikamu koma zikangoyamba kusowa, kukhala mavuto adzaoneni. Boma likadapanga zoti zinthu zisadafike poterepa, chimanga chifikiretu mmisika ya Admarc, adatero Kalowekamo. +Chisomo Mwale wa ku area 25 mumzinda womwewu, adati polingalira nyimbo ya nthawi zonse ya manyamulidwe a chimanga popita mmisika ya Admarc, bungwe la Admarc likuyenera kupangiratu ndondomeko zoyenera. +Vuto lalikulu lomwe limakhalako nkulephera kukonzekera mokwanira. Mwachitsanzo, misika ya Admarc ikayamba kugulitsa chimanga kumakhala nkhani zosakhala bwino monga za chinyengo, nkhanza ndi mavuto a zamayendedwe. Ino ndiye nyengo yabwino yokonza zinthu ngati zimenezi, adatero Mwale. +Pa za tsiku lotsegula misika ya Admarc ndi kukonzekera kuthana ndi mavuto omwe anthu akuti amakumana nawo pokagula chimanga, mneneri wa bungwe la Admarc Agnes Chikoko adangoti titsate zomwe idanena nduna. +Koma nduna ya zachuma Goodall Gondwe adati anthu asade nkhawa kwambiri pankhani yopeza chimanga chifukwa boma lakhazikitsa ndalama zokwana K13.2 biliyoni zoti zithandize anthu ovutika kupeza ndalama zogulira chimanga kudzera mupologalamu yogwira ntchito zachitukuko ndi yothandiza anthu okalamba ndi ovutikitsitsa. +Mavuto onsewo tidawawerengera kale moti panopa tawonjezera thumba la ndalama zomwe anthu amalandira akagwira ntchito zachitukuko za Public Works Programme komanso zomwe timapatsa anthu ovutika kwambiri podzera mupologalamu ya Social Cash Transfer, adatero Gondwe. +Iye adati K11 biliyoni ndi ya pologalamu ya ntchito zachitukuko pomwe K2.2 biliyoni ndi yogawira anthu ovutikitsitsa mupologalamu ya Social Cash Transfer yomwe cholinga chake chenicheni nkuthandiza anthu kugula chimanga. +Malungo atheretuUnduna Pamene dziko limakumbukira ntchito yothana ndi malungo Lachiwiri, boma la Malawi lati likuyesetsa kuti malungo mdziko muno atheretu. +Bungwe la zaumoyo pa dziko lonse la World Health Organisation (WHO) lidapatula 25 April chaka chilichonse kukhala tsiku lokumbukira nthendayi, imene imatengera kuli chete anthu ambiri, makamaka amayi oyembekezera ndi ana a mu Africa.aria Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ndipo pamene mutu wa chaka chino Kuthetseratu Malungo ukukhudza dziko la Malawi kwambiri, WHO idalengeza kuti dziko lino, limodzi ndi Kenya komanso Ghana, akhala maiko oyamba padziko lapansi kulandira katemera wa malungo kuyambira chaka cha mawa. +Woimira WHO pankhani yolimbana ndi malungo mdziko muno, Wilfred Dodoli adati ndondomeko ya katemerayu ndi yongoyesera chabe koma wati ali ndi chikhulupiliro kuti ndi wothandiza makamaka kwa ana. +Uku nkubowoleza chinsinsi chothana ndi malungo. Tikuyembekezera kuti ana 120 000 a pakati pa miyezi isanu ndi 25 mmadera osankhidwa alandira katemerayu, adatero iye. +Unduna wa zaumoyo wati katemerayu athandiza kuchepetsanso imfa zodza ndi malungo ndi pafupifupi 40 pa imfa 100 zomwe zimagwa pakati pa ana ndi chiyembekezo choti mtsogolo muno vutoli lidzatheratu. +Undunawu watinso wakhazikitsa kafukufuku wofuna kupeza momwe vuto la malungo lilili mdziko muno pofuna kuonjezera mapologalamu ena oyenera kuti dziko la Malawi likwanitse cholinga cha mutu wa chaka chinowo. +Mkulu woyanganira ntchito zaumoyo muunduna wa zaumoyo Dr Charles Mwansambo wati kafukufukuyu achitika mmadera osankhidwa ndipo achitidwa ndi madotolo omwe adaphunzitsidwa bwino ntchito ya zaumoyo makamaka zokhudzana ndi malungo. +Kafukufukuyu akhudza kuunika kagwiritsidwe ntchito ka masikito otetezedwa, kaperekedwe ka thandizo la mankhwala a malungo, kuyeza malungo ndi kuchuluka kwa magazi mmatupi mwa ana omwe atenge nawo gawo mu kafukufukuyu, adatero Mwansambo. +Mu uthenga wa tsiku lokumbukira matenda a malungo, unduna wa zaumoyo udati mzaka zisanu zapitazi, imfa zodza ndi malungo zachepa ndi 60 pa imfa 100 zomwe zinkachitika ndipo undunawu wati ichi nchifukwa cha kuyenda bwino kwa mapologalamuwa. +Chifukwa cha mapologalamu monga kugawa masikito onyikidwa mmankhwala, kupopera mankhwala mmakomo ndi kulimbikitsa amayi oyembekezera kuyezetsa malungo ndi kulandira thandizo nthawi yabwino, imfa zodza ndi malungo zatsika, chidatero chikalatacho. +Mkulu wa bungwe la zaumoyo la Malawi Health Equity Network (MHEN) George Jobe wati ndondomeko zomwe unduna wa zaumoyo uli nazo ndi zabwino. +Iye adati njuga yagona pa momwe ndondomekozi zikuyendetsedwera ndi maphunziro a zaumoyo omwe anthu akulandira kuti azitha kutsatira bwino ndondomekozi kuti zipindule. +Ndondomekozi nzabwino koma mpofunika kuunika kuti anthu akuphunzitsidwa mokwanira? Ndikunena izi polingalira zomwe zikuchitika mmaderamu kuti ena akugwiritsa ntchito masikito omwe amalandira powedzera nsomba ndi kupangira madimba, adatero Jobe. +Senior Chief Mwadzama ya ku Nkhotakota idavomereza kuti pakadali vuto lalikulu pakati pa anthu kutsatira malangizo makamaka pakagwiritsidwe ntchito ka masikito a udzudzu ngakhale kuti pangonopangono anthu ayamba kumvetsetsa. +Poyamba kudali zikhulupiliro zoti mankhwala a masikitowa amafowola anthu koma pano ambiri akumvetsetsa kufunika kogona mmasikito. Tidakhazikitsanso malamulo kuti opezeka akugwiritsa ntchito masikito powedzera nsomba kapena kupangira dimba, tizimulambalala pakabwera mapologalamu ena ndiye anthu akuwopa, adatero Mwadzama. +Padakali pano, nduna ya zaumoyo Peter Kumpalume yati dziko lino lasayina pangano ndi dziko la China kuti akatswiri a ku China abwere kudzathandiza pakafukufuku wa mankhwala a zitsamba ochiza malungo. +Mankhwalawo alipo ndipo timawagwiritsa ntchito, koma tikufuna kupeza kuti mankhwala omwe angagonjetse malungo ndi ati ndipo tingawakonze bwanji mmafakitale kuti akhale osavuta kugwiritsa ntchito, adatero Kumpalume Dziko la China lidagonjetsa kale malungo ndipo wachiwiri kwa nduna ya zaumoyo ndi kulera mdzikolo Wang Guogiang adati izi zidatheka pogwiritsa ntchito mankhwala a zitsamba. +Akufuna fisi alangidwe koopsa Magulu omwe amalimbikitsa maufulu a amayi ati mpofunika mkulu woimira boma pa milandu Director of Public Prosecutions (DPP) Mary Kachale atengere nkhani ya Eric Aniva kubwalo lalikulu. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Aniva, yemwe adanjatidwa zaka ziwiri kukagwira ntchito ya kalavulagaga kundende atapezeka wolakwa pamlandu wotenga mbali pa miyambo yoopsa pokhala fisi wochotsa fumbi ndi kulowa kufa mboma la Nsanje. +Adampatsa zaka ziwiri: Aniva Nkhani ya Aniva idagwedeza dziko atabwera poyera nkuulula kuti wakhala akugwira ntchito ya ufisi kwa nthawi yaitali ndipo adagonana ndi amayi ndi atsikana oposa 100. +Koma magulu a amayi, motsogozedwa ndi mabungwe a Malawi Human Rights Resource Centre (MHRRC), NGO Gender Co-ordination Network (NGO-GCN) ndi African Womens Development and Communications Network (Femnet), ati chigamulo chomwe Aniva adalandira lachiwiri lapitali nchochepa. +Maguluwa ati potengera mlandu wa Aniva, ufulu wa amayi sudalemekezedwe kotero amayenera kulandira chilango chokhwima osati zaka ziwiri basi. +Ndife okhudzidwa kuti munthu yemwe ali ndi kachilombo ka HIV komwe kamayambitsa matenda a Edzi ndipo amapitiriza kugona ndi amayi ndi ana achichepere mpaka zaka 12 angalandire chilango chochepa chonchi. +Ndi uthenga wanji omwe tikupereka kwa abambo ena akhalidwe longa lomweli? Zaka ziwiri basi mlandu wonsewu? Uku nkunyoza amayi ndipo bwalo la milandu likuyenera kuunikapo bwino nkusintha chigamulochi, adatero mkulu wa bungwe la MHRRC Emma Kaliya. +Mabungwewa adati ngati nkhani yoyamba ya mtunduwu yoweruzidwa pogwiritsa ntchito lamulo latsopano la za ufulu wa anthu, Aniva amayenera kulandira chilango choletsa khalidweli. +Naye mkulu wa zophunzitsa anthu kubungwe la Femnet, Hellen Apila, adati apa dziko la Malawi waphonya mwayi waukulu wopera chenjezo kwa anthu omwe salemekeza ufulu wa amayi potsatila miyambo. +Bwalo la Magistrate ku Blantyre lidagamula Aniva lachiwiri lapitali kuti akagwire ntchito yakalavulagaga kundende atavomera kuti amachita mwambo wa fisi akudziwa kuti ali ndi kachilombo ka HIV. +Aphungu aunguza njira zokhaulitsira auve Uve wanyanya mdziko muno koma pano zafika poti wina akalowa nazo kundende! Nyumba ya Malamulo yati nyansi zamgonagona zomwe zili mmakhonsolo osiyanasiyana zikubweretsa fungo loipa komanso zikuika moyo wa anthu pachiwopsezo. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Pachifukwa ichi, aphungu a ku Nyumbayi agwirizana zoti akambirane zokhazikitsa malamulo omwe azipereka mphamvu zonjata munthu wopezeka akuchita utchisi. +Nkhaniyi idalandiridwa ndi manja awiri ndi aphungu osiyanasiyana phungu wa pakati mboma la Lilongwe Lobin Lowe ataiyambitsa Lachinayi mNyumbayi. +Lowe adati nzokhumudwitsa kuti fungo loipa lili ponseponse mmakhonsolo kaamba koti akuluakulu ake amalephera kuchotsa zinyalala komanso zoipa zochoka mmakampani ndi mmafakitale zikumathera mmitsinje. +Iye adati izi zikuchitika kaamba koti palibe lamulo loletsa anthu kuchita uve monga momwe zimakhalira mmaiko ena. +Vuto ndi loti tilibe malamulo ngati mmaiko a anzathu nchifukwa chake anthu amangotaya zinyalala chisawawa ngakhale kukodza kumene anthu amangokodza momwe afunira chifukwa palibe chilango chilichonse chomwe angalandire, adatero Lowe. +Phungu wa ku Mpoto cha ku Madzulo kwa boma la Salima, Jessie Kabwila, adavomereza izi ponena kuti chomvetsa chisoni kwambiri nchakuti akuluakulu ena amaphunziro awo akuchita nawo uve woterewu. +Iye adati uve wotere kuulekerera ukhoza kusokoneza ntchito zokopa alendo kaamba koti anthu obwera amafuna malo ndi zinthu zaukhondo kuopa woyandikana nawo nyumba. +Lipoti loyamba likusonyeza kuti iye adayamba kugonana ndi ana akewo mchaka cha 2014 kutanthauza kuti wina ali ndi zaka 6 pomwe wina adali ndi zaka 4, Namwaza adatero. +Chiyambireni zolaulazi, mkuluyo akuti wakhala akuopseza ana akewo kuti asadzayerekeze kutsina khutu aliyense za nkhaniyi. Koma poti amati tsoka chimanga chilinda moto, anawo adatopa ndi uvewo. +Namwaza adati aka si koyamba kuti mkuluyo amveke ndi mbiri yomwa mazira akewo. +Akuti mayi wa anawo, yemwe ndi mkazi wake, adawapezapo mwezi wa October chaka chino akuluwo ali ndi mwana wa zaka 7 akupanga naye zadama, koma banjalo lidakambirana za nkhaniyo ndipo idangofera mmazira. +Akutitu atakambirana, bamboyo adapepesa komanso adaopseza mayiyo kuti akadzangoyerekeza kuulula adzamukhaulitsa ndiye chifukwa cha mantha, adakhaladi chete, adatero Namwaza. +Iye adati koma pa November 22 ndi pomwe oyandikana nawo nyumba adalimbikitsa mayiyo kukanena nkhaniyi kupolisi. +Namwaza adati anawo adapita nawo kuchipatala cha Kasungu komwe adakawayesa ndi kuti akalandire thandizo ngati nkoyenera ndipo apolisi akuyembekezera zotsatira. +Tsiku lomwe mwanayo adakaulula za khalidwe la bamboo akewo ndi lomwe bwalo la milandu la magisitireti mumzinda wa Blantyre lidagamula Eric Aniva, fisi wa ku Nsanje, kuti akagwire ndende zaka ziwiri. +Magulu osiyanasiyana, makamaka omenyera ufulu anthu, sadakondwe ndi chigamulochi ponena kuti ndi chochepa ndipo chosakwanira kuthetsa khalidwe lophwanya ufulu wa amayi ndi asungwana. +Mmodzi mwa omwe adadzudzula chigamulochi ndi mkulu wa bungwe la Malawi Human Rights Resource Centre (MHRRC) Emma Kaliya yemwe adati chigamulochi nchosaopsa kwa abambo akhalidweli. +Mkuluyu amachokera mmudzi mwa Chiswe, mfumu yaikulu Chikumbu mboma la Mulanje ndipo apolisi ati adzaonekera kukhothi kafukufuku akatha. +Anachezera Zidatheka! Zikomo Anatchereza, Ndafuna ndikuthokozeni kwambiri chifukwa cha malangizo anu. Pano tidamanga banja ndi mtsikana wa ku Machinga uja ndipo pano tikukhala ku Phalombe bwinobwino. Ndathokoza pondithandiza maganizo. +Chifundo Makisi, Phalombe Zikomo a Makisi, Nkhani yosangalatsa! Inenso ndathokoza kwambiri kuti mutatsatira malangizo anga mwalongosola zonse za banja ndipo pano zonse zatheka bwinobwino. Zonyandiritsa kwambiri. Izi ndi zimene timafuna, paja amati mutu umodzi susenza denga. Munthu ukazingwa umayenera kupempha nzeru kwa ena monga akuluakulu ndipo nthawi zambiri malangizo awo amakhala aphindu ukawatsatira. Ndiye ndasangalala zedi kuti ndinatha kukuthandizani pamoyo wanu wa banja. Ambuye akutsogolereni mzonse kuti banja lanu likhale lolimba ndiponso langwiro komanso lachitsanzo kwa ena. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Amanditukwana Ine ndidapeza mwamuna woti timange banja koma tikuyendetsa chibwenzi, khalidwe lake amangonditukwana ndi abale anga ngati anafuna kuti tionane ine nkulephera. Agogo, ndithandizeni, kodi pamenepa nditani? AM Area 49, Lilongwe Zikomo AM, Pa Chichewa pali mawu oti ali dere nkulinga utayenda naye. Ndikhulupirira tanthauzo la la mawu amenewa umalidziwa. Mwachidule, ndinene kuti kufunikira kokhala pachibwenzi anthu musanakwatirane nkoti mumatha kudziwana makhalidwe ndi zofuna musanaganize zolowa mbanja. Khalidwe ndi lofunika kwambiri paumunthu. Tsono munthu wakhalidwe labwino ungamudziwe bwanji? Munthu wakhalidwe labwino ndi woti sachita kapena kunena zinthu zodandaulitsa kwa ena. Wakuba, wachiwerewere, wotukwana, wamiseche, waumbombo kapena wochita zinthu zina zolaula tinganene kuti ndi wamakhalidwe abwino? Osatheka! Ndiye apa wadzionera wekha khalidwe la bwenzi lakolokukonda kutukwana. Kodi mukadzakwatirana adzasintha khalidwe limenelo? Kaya! Uyu wadzionetsa kale mawanga ake ndipo usataye naye nthawi, musiye chifukwa si munthu womanga naye banja ameneyo. Munthu wotukwana mkazi kapena abale ake ndi munthu wopanda khalidwe. Ndiye iyeyo ungalimbe mtima kukwatirana ndi munthu woteroyo? Ine ndikuti asakutayitse nthawi, peza wina wamakhalidwe abwino. +Ndinalakwitsa kumuuza? Agogo, Ndakhala pachibwenzi ndi mkazi wina kuyambira 2012 koma pamene ndinkamufunsira nkuti ndikumwa ma ARV koma chaka chino mpamene ndamuuza kuti ndili choncho. Padalibe kusintha pachikondi chathu koma vuto lidabwera atapita ku Blantyre. Ali konko andandiuza kuti adakayezetsa magazi ndipo sadamupeze ndi kachilombo ka HIV. Kuchokera pompo chikondi chidasintha, sitimakondana monga mwakale moti pano adakali ku Blantyre. Kodi mwina ndidalakwitsa kumuuza za mmene ndilili? Chonde ndithandizeni. +Ana avala umasiye Makolo akali moyo Nthawi ya nkhomaliro yakwana, pamsika wa Manje mumzinda wa Blantyre ambiri akudya nsima pamene ena akusaka chakudya. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kuponya maso patali pali ana atatu, Fakili wa zaka 8, Pemphero, 7, ndi Yamikani 4. Pemphero lawo nkuti apeze chakudya. Anawa aima pafupi ndi mpanda wa mfumu Misesa. +Tikufuna tipemphe mango, tilibe chakudya, adatero Fakili, uku akutonthoza Yamikani amene akulira chifukwa chomukaniza kutoleza makoko a mango. +Uwu ndiye umasiye omwe anawa auvala makolo awo ali moyo. Zonsezo zikuchitika chifukwa makolowo sakumwetsana madzi. Kumenyana kwa njobvu, wovutika ndi udzu. +Fakili akulephera kufotokoza bwinobwino chomwe chidachitika kuti ayambe kukhala moyo wovutika choncho. +Fakili (Kumanja) ndi abale ake Yamikani ndi Pemphero Amayi sakutifuna. komanso ababa adachoka koma pena amatisaka, adatero iye. +Mfumu Misesa ikuti anawa si achilendo mdera lake. +Gulupuyu akuti patha mwezi anawo akungoyendayenda mdera lake. Kunyumba kwanga agona masiku awiri, adatero iye. +Uko atawathyolera mango kuti azikukuta, Misesa adati banja la makolo a anawo lidatha ndipo kuchokera pa nthawiyo, anawo akhala akuzunzika. +Ndidawaitana onse kuti tikambirane koma zidakanika. Mkazi akuti iye adapeza banja lina ndipo sangasunge anawa pamene bamboyo ali ndi chidwi chowasunga koma akuti sangathe chifukwa alibe pokhala komanso ntchito idatha, adatero Misesa. +Lolemba Msangulutso udakumana ndi bambo wa anawa. Bamboyo, Dave Singano adati mtima wosunga anawo ali nawo koma sangathe chifukwa alibe thandizo. +Zikundiwawa kuti anawa akuzunzika komabe palibe chomwe ndingachite chifukwa ndilibe thandizo. Ndilibenso pogona, ndiye ngakhale ndiwatenge akagona potani? adatero Singano. +Bamboyu adati patha zaka zitatu chisiyirane ndi mkazi wake. Iye adati adathetsa banja lake pomuganizira mkaziyo kuti akumuyenda njomba. +Panthawiyo ndinkagwira ntchito ya ulonda. Ndiye anthu ena adanditsina khutu kuti ndikachoka kukumabwera mwamuna mnyumbamo. Nditakambirana ndi mkazi wanga sitidamvane ndipo banja lidatha, adatero. +Singano akuti adagwirizana ndi mkazi wake komanso amfumu kuti anawo akakhala ndi mkaziyo ndipo iye azipereka thandizo. +Panthawiyo zidachitika momwemo, koma kungotha miyezi yochepa adasintha pamene adati sangakwanitse kukhala ndi anawo poti wapeza mwamuna wina. +Ndidakhala ndi anawo komabe nanenso zidandisokonekera, ntchito idatha, adandichotsa palendi. Ndikadatani? adatero Singano. +Iye adati patha chaka chimodzi tsopano anawa akukhala wokha, komabe ndikapeza thandizo ndimawasaka. Monga dzana [Lamulungu] ndidawatenga ndipo ndidakagona nawo ku Chilobwe kwa mnzanga, adatero iye. +Naye mkazi wa bamboyu akuti adauza bwalo la mfumu Misesa kuti sangatenge anawo chifukwa adakwatiwanso. +Adauza bwalo kuti anawa sakuwatenga, patsikulo adabwera ndi mwamuna wake watsopanoyo. Nditamuitananso kuti tidzakambirane sadabwere mpaka lero, adatero Misesa. +Gawo 60 loteteza ana, limati kholo lolephera kusamala ana ake liyenera kunjatidwa. +Misesa akuti nkhaniyi idapita kupolisi ndipo apolisi adanjata bamboyo koma adamutulutsa tsiku lomwelo. +Koma mkulu womenyera ufulu wa ana kubungwe la Centre for Childrens Affairs Malawi, Moses Busher adadzidzimuka ndi nkhaniyo ndipo adati makolowa akuyenera kunjatidwa. +Iye adati bungwe lawo litengera nkhaniyo kukhoti la ana. Ngati bungwe lomenyera ufulu wa ana, nkhaniyo sitiyisiya mpaka anawa athandizidwe. Mayi akuyenera kusunga anawo mosayangana kuti wakwatiwa kapena ayi ndipo bamboyo akuyenera kumawathandiza. Tifufuza ndipo ana amenewa athandizidwa, adatero Busher. +Atafunsidwa ngati ndikololedwa kuti anawa atengedwe ndi banja lina kukawasunga ngati ana awo, Busher adati ndizotheka pokhapokha ndondomeko itatsatidwa. +Koma poona kuti makolo awo onse alipo ndipo izi zangochitika chifukwa cholekerera, zifukwa zotenga anawa kukhala ako sizikumveka, adaonjeza. +Pamene mutu wa nkhaniyi ukufufuzidwa, moyo wa anawo udakali pamavuto adzaoneni. +Kusukulu sapita, pogona ndi kubowo kwa uvuni ya njerwa, mkalasi, apo ayi apemphe pakhomo pa eni. Chakudya chawo ndi mango, misonga ya mzimbe ndipo akadya bwino ndiye kuti banja lina lawagawira. +MEC igwira njakata pa zisankho zapadera Zinthu sizikuyenda kubungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) komwe tsogolo la zisankho zapadera silikudziwika. +Lachitatu lapitali, mkulu wa nthambi yoona za chuma kubungweli, Linda Kunje, adauza Tamvani kuti zisankho zachibwereza zichitikabe mtsogolo muno koma tsiku lenileni silikudziwika. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mathanga: Tikudikirabe ndalama kuchokera kuboma Posachedwa bungwe la MEC lidatulutsa chikalata chodziwitsa onse okhudzidwa ndi zisankhozi kuti ayamba aziimitsa kaye kaamba koti boma silidapereke ndalama zoyendetsera zisankhozi, zomwe zikuyembekezeka kuchitika ku Mchinji West Constituency, Kaliyeka Ward ku Lilongwe City South East Constituency, Sadzi Ward ku Zomba Central constituency, Bunda Ward ku Kasungu Central Constituency ndi Bembeke Ward ku Dedza South Constituency. +Mmodzi mwa makomishona kubungweli, Jean Mathanga, akuti pakufunika zosachepera K499 miliyoni zoyendetsera zisankhozi. +Mathanga adati boma silidawapatse ndalamazo koma adatsimikiza kuti zisankhozi zichitikabe mtsogolo muno. +Koma mneneri wa nthambi yoona za chuma kuboma, Nations Msowoya, watsindika kuti boma silipereka ndalama ku MEC pokhapokha lipoti lofotokoza za kusokonezeka kwa ndalama kubungweli litatulutsidwa. +Msowoya: Boma silipereka msanga ndalama Ife tidapempha kuti pakhale kafukufuku pa momwe ndalama zidayendera ndipo chomwe tikudikira ndi lipoti. Akatipatsa lipotilo, ndipo tikakhutitsidwa nalo tikhala okonzeka kupereka ndalamazo, adatero Msowoya. +Mchaka cha 2012 mpaka 2014, kubungweli kudasowa ndalama zoposa K15 miliyoni. Kusowa kwa ndalamazi kudachititsa kuti akuluakulu ena kubungweli akakamizidwe kuti akapume kaye ndi cholinga choti afufuze bwino za mmene ndalama zosowazo zidayendera. +Pa 24 August chaka chino, MEC idatumiza akuluakuluwo, omwe ndi mkulu wa zisankho Willie Kalonga, komanso Harris Potani, George Khaki, Khumbo Phiri, Edington Chilapondwa, Chimwemwe Kamala, ndi Sydney Ndembe kuti abapuma kaye pomwe zofufuzazo zili mkati. +Zitachitika izi, mu August momwemo, boma lidalemba anamnadwa atatu, Rex Harawa, Stevenson Kamphasa ndi Duncan Tambala kuti achite kafukufuku pa kusokonekera kwa ndalamazo. +Koma izi zili chonchi, Kunje akuti zisankho zikhalapobe posakhalitsapa. +Mitima ya anthu ikhale mmalo. Ngakhale sitingalonjeze tsiku lenileni lomwe zisankhozi zidzachitike, zichitika ndithu posakhalitsa, adatero iye. +Si izi zokha, kumwaliranso kwa wapampando wa MEC, Maxon Mbendera, ndi komwe kukukayikitsa ngati bungweli lingapangitse zisankho posakhalitsa. Koma malinga ndi Kunje, ili si vuto. +Kulingalira malumbiro Abale anzanga, tidakhala pa Wenela kuonera kulumbiritsa kwa atsogoleri. +Woyamba kulumbiritsidwa adali Adama Barrow wa ku Gambia. Musandifunse kuti ameneyu ndidamudziwa bwanji, chifukwa sindikuyankhani. Mumafuna mumudziwe nokha? Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mwinatu sindidanene. Gambia ndi dziko limene anthu ake adachokera ku Zambia, muja anthu a ku Malawi adachokera ku Malaysia ndipo a ku Austria adachokera ku Australia! Ndife amodzi. +Tsonotu Barrow adalumbilitsidwa kuofesi ya kazembe wa Gambia ku Senegal patatha sabata zingapo atakwapula mkulu uja Yahaya Jammeh pachisankho. Bolatu kwa anzathu amakhala sabata zingapo wina asanalumbire koma pano pa Wenela usiku siudutsa! Mwaiwala kale muja Moya Pete adalumbirira? Uyu Barrow adalumbira ku Senegal paja chifukwa Yahaya amakana kuchoka pampando. Demokalase ndiye imeneyo! Yaponda yamwa! Yalakwa yalakwa! Yahaya adaziona. +Tsono sindikamba za kulumbira mdziko la eni. Kodi pa Wenela wina atakana kuti sanapambane pachisankho, wosankhidwa angakalumbire ku Mpanyira patsidya pa Tsangano? Zingatheke wosankhidwa pa Wenela kukalumbira ku Mbeya kapena Masvingo chifukwa sizingatheke pabwalo la pa Wenela? Winatu amalumbira adali mkulu uja Donal J Trump. Pajatu K2 000 ikutchedwa Trump chifukwa cha kukula mtima kwake. Iyetu adalumbira atagwira mabaibulo awiri. Loyamba lidali la mkulu wamtali uja, Abraham Lincoln. Kukadakhala kuno, bwenzi tikuti Moya Pete adalumbira atagwira baibulo lija adalumbirira gogo uja adandipeza ndikulima kwathu kwa Kanduku. +Koma zingatheke? Ndipo popita kokalumbira, Trump adayamba wamwa tiyi ndi uyu akutulukayu, Barrack Obama. Kenako, onse adakwera galimoto imodzi. Kuno kwathu zingatheke? Abiti Patuma ndi Moya Pete kukwera galomoto limodzi? Tsonotu sindili pano kukamba za Barrow kapena Trump. Yanga nkhani ndi ya Saulo Chagalauza. Pajatu mkuluyo adabwera ndi moto, kukamba zosintha zinthu kuphiri. +Mkuluyu lero wangoti ziiii! Sakukambapo kanthu za Joloji Mmera Chadyaka mkulu amene wafufuta chimanga chopezeka pambendera ya Dizilo Petulo Palibe, adatero Abiti Patuma. +Palibe chimene ndidatolapo. +Komatu Chadyaka adya ndalama zambiri. Nanga umboni wakuti adanyambita khusa uli kuti? adafunsa Gervazzio, akuika nyimbo ya Lucius Banda: Mabala. +Malume ndalama kubisa kubanki Pamene Mbumba yawo ikufa ndi njala Adya ndalama bwanji? Zonsetu tiziona mwezi uno ukamatha chifukwa ndiye tsikulo kuli kokakatula ndi sizala, adatero Abiti Patuma. +Adandipindanso. +Chomwe ndikunena, uyu Saulo akupenya, akumva ndipo pakamwa ali napo koma sakulankhula. Watsamwa. Mwinatu akuopa Chadyaka paja mpandowu ngolimbirana. Ndani safuna kukhala Barrow kapena Trump? 2019 ndi chaka chinacho, adatero Abiti Patuma. +Kulira, chimwemwe ndi banki mkhonde Ngakhale adali ndi chidwi choyamba bizinezi kuti atukuke, kusowa kwa mpamba kumapondereza khumbolo. Sanderson Yuba wa mmudzi mwa Namalima kwa T/A Nazombe mboma la Phalombe adakanika kutenga ngongole kubanki kaamba kosowa chikole komanso kuopa chiongola dzanja chokwera. +Lero mkuluyu ndi mmodzi mwa makhumutcha mderalo kutsatira ngongole yomwe adatenga kubanki mkhonde ndi kuyamba bizinezi ya matabwa mpaka wamanga nyumba ya malata, kugula njinga ya moto ndi ziweto. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mabanki mkhonde afalikira mdziko muno Kupanda banki mkhonde loto langa loyamba bizineziyi si likanakwaniritsidwa. Bwenzi pano ndili mpopangolo wa mmudzi. Bankiyi idandithandiza kupeza mpamba, adatero Yuba. +Yuba ndi mmodzi mwa Amalawi omwe miyoyo yawo yasintha chifukwa cha mabankiwa. Koma si onse otenga nawo mbali akusimba lokoma, ena akumana ndi zikhomo kutsatira kusokoneza ngongole zawo za banki mkhonde ndipo ali muumphawi. +Mmodzi mwa iwo ndi Janet Mawata wa mboma la Phalombe lomwelo yemwe atakanika kubwenza ngongole ya K20 000 adalandidwa katundu. +Mayi wina, yemwe anati tisamutchule dzina, ku Zomba adalandidwa nyumba kaamba ka ngongole ya K250 000 ndipo padakalipano umoyo wake ukuvuta. +Pakutha pa chaka, mmizinda ndi mmatauni anthu akumagawana ndalama zochuluka, ena mpaka K7 miliyoni, kuchoka kubanki mkhonde. Koma ndalamazi zimasungidwa mnyumba mwa membala wosankhidwa kutero, osati kubanki. +Izi zidachititsa mkulu wakale wa banki yaikulu mdziko muno ya Reserve Bank of Malawi (RBM), Charles Chuka kunena kuti mabanki mkhonde sakufunika chifukwa akusokoneza kayendedwe ka chuma. +Mabungwe ena atsutsa izi. +Mkulu wa Community Savings and Investing Promotion (Comsip) bungwe lomwe limayanganira mabanki mkhonde, Tenneson Gondwe, adati kutero ndi kusokoneza cholinga cha ndondomekoyi yomwe imapereka mpata wa ngongole kwa anthu osowa. +Anthuwa amasonkha ndalama zomwe amabwerekana ndi kuyamba mabizinezi komanso kugawana pakutha pa chaka. Kulowerera kwa RBM kungasokoneza miyoyo ya anthu. Ngati akufuna angopanga banki ya kumudzi yomwe izikwaniritsa zosowa za anthu, adatero Gondwe. +Kafukufuku wa bungwe la Finscope adapeza kuti anthu 50 pa 100 ali onse mdziko muno ali ndi kuthekera kofika ku mabanki a pamwamba koma 21 pa 100 wo ndi amene ali ndi mabuku ku mabankiwo. +Zotsatirazi zikupereka mpata kumabanki mkhonde kukhala ndi anthu ochuluka poonjezera chiongola dzanja chochepa chomwe amapereka pa ngongole iliyonse. +Mbusa amuganizira kugwirira wozelezeka Apolisi mboma la Neno akusunga mchitokosi mbusa wina wa zaka 52 yemwe amatchuka kutyi Pastor Joshua wa mpingo wa United of God pomuganizira kuti adagwirira mtsikana wodwala nthenda yakugwa wa zaka 16. +Mbusayo, yemwe dzina lake lenileni ndi Juwayo Antoniyo amachokera mmudzi mwa Siyali Traditional Authority(T/A) Chapananga mboma la Chikwawa. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Malinga ndi mneneri wa apolisi mboma la Neno Raphael Kaliati, Antoniyo adakumana ndi mtsikanayo Lachisanu pa May 5 akuchokera ku chigayo. +Mtsikanayo adaima panyumba ya mbusayo kupemphako madzi akumwa, ndipo mbusayo adamuuza kuti angolowa nkukamwera madziwo mnyumbamo. Apa adamutsatira mtsikanayu ndi kumugwiririra, adatero Kaliati. +Iye adati mtsikanayo adakamuneneza mbusayo kwa mayi ake omwe adakadandaula kupolisi. +Kalata yaku chipatala yatsimikiza kuti mtsikanayu adagwiriridwadi, adatero Kaliati. +Malinga ndi apolisiwa mbusayo aonekera kubwalo la milandu masiku akubwerawa. +Izi zakhumudwitsa mamembala a mpingowu. +Mkucheza kwathu ndi Traditional Authority Mlauli yemwenso ndi mmodzi mwa anthu omwe amapemphera mumpingowo, adati chokhumudwitsa nchoti mtsikanayu amagwa. +Mlauli adati mbusayo adayamba mpingowu mchaka cha 2014 ndipo anthuwa amamukhulupirira. +Mbusayotu amaonetsa ngati weniweni mzochitika zake. Nthawi zina amakafika mpaka ku Tete mdziko la Mozambique kukalalikira, choncho titamva kuti wagwidwa pokhudzidwa ndi nkhaniyo, tazunguzika, adatero Mlauli. +Iye adati Antoniyo wabwerera kuchoka ku Mozambique chaka chathachi. +Mlauli adaonjezera kuti mbusayu wasiya anthu opemphera pa mpingowo pa umasiye. +Ife pakutivutanso ndi poti iyeyu adayambitsa mipingo ku Mulanje komwe iliko iwiri, ku Ndirande mumzinda wa Blantyre, ku Zomba ndi ku Chikwawa, kodi nkhosa zake mmadera onsewa zitani, adadandaula motero Mlauli. +Mbusayu ali pa banja. +Agumula nyumba pokaikira masalamusi Mbuto ya kalulu idakula ntadzaonani. Mwambiwu udapherezera Lachiwiri ku Lilongwe pomwe anthu okwiya ku Mtsiriza adagumula nyumba ya banja lina ati powaganizira kuti amazembetsa anthu mmatsenga. +Anthuwo sadalekere pomwepo, koma kuotcha galimoto lapolisi lomwe apolisi adakwera kuti akateteze banja la Malunga amene adaotcheredwa nyumbayo. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mneneri wa likulu la apolisi James Kadadzera watsimikiza za chipolowecho ndipo wati apolisi agwira anthu 20 omwe akuwaganizira kuti akukhudzidwa pa chipolowecho. +Kadadzera: Tilibe lipoti Awa tawagwira ngati poyambira kafukufuku ofuna kupeza chenicheni chomwe chidachitika chifukwa pakumveka nkhani zosiyanasiyana ngakhale mphekesera yaikulu ikukhudza za masilamusi, adatero iye. +Polankhula ndi Msangulutso, anthu omwe adaona izi zikuchitika adati banjalo amalikaikira kuti limasowetsa anthu mmatsenga ndipo patsikulo, munthu wina yemwe amalira momvetsa chisoni adawauza kuti Mulungu adamuonetsa vumbulutso akupephera kuti mbale wake yemwe adasowa akusungidwa mnyumbamo. +Mmodzi mwa anthuwo, Enifa Kaira, adati mphekeserayo itamveka anthu adayamba kusonkhana panyumbapo uku akukalipa kuti eni nyumbayo atulutse anthu onse omwe amawasunga mmatsenga. +Kudali khamu la anthu: Ana, akulu ndi okalamba kufuna kuonetsetsa kuti mnyumbamo mutuluka chiyani. Eni nyumbayo ataona kuti zinthu zikuonjeza, adamuuza odandaulayo kuti alowe mnyumbamo akayangane mbale wakeyo koma naye sadatuluke mpaka apolisi adafika, adatero iye. +Kaira adati apolisi atafika adathamangira mnyumbamo ndipo potuluka adatenga odandaulayo ndi eni nyumbayo nkuwakweza galimoto ya polisi kuti azipita nawo koma anthu sadakondwe nazo ndipo adayamba kugenda apolisiwo nkuwayatsira galimotoyo. +Mwana wamkulu wa mnyumbamo Mwayi Malunga, wa zaka 24, yemwe adali pakhomo pomwe izi zimachitika adati zomwe anthuwo adachita lidali dumbo chabe poti anthu mderalo safunira banjalo zabwino. +Iye adati pomwe zonse zidayamba mma 3 koloko masana iye akupuma ndipo amamvera phokoso la anthu kutulo osadziwa kuti kukuchitika chiyani mpaka pomwe mayi ake adamudzutsa kuti akaone zomwe zikuchitika kunja. +Malunga adati atatuluka panja adaona khamu la anthu likusokosa uku likuloza nyumbayo pakati pawo pali munthu wa mtsikana akulira uku akuti akufuna mbale wake yemwe ali mnyumbamo. +Pokana milandu, tidamupatsa mwayi woti alowe mnyumbamo ayangane paliponse ndipo adafufuzadi koma osapeza kanthu kenako tidangoona wagwa nkukhala ngati wakomoka mpaka pomwe apolisi amafika, adatero Malunga. +Iye adati apolisiwo akuti azinyamuka ndi munthuyo komanso makolo ake, anthu adayamba kuwakuwiza kenako kugenda koma apolisiwo adaliza galimoto yawo ndipo asadafike patali, anthuwo adayiyatsa iwo nkuthawa. +Mnyamatayo adati anthuwo adayamba kugenda nyumba yawo mpaka kuswa magalasi onse, chitseko komanso ena adakanganula malata mbali imodzi nkugwetsa mpanda wa njerwa komanso kuzula chitseko cha mpandawo nkunyamula. +Zidali zachidziwikire kuti kwinako zidalowa kuba basi osati zomwe amanenazo chifukwa mpaka pano munthu yemwe amati tikusungayo sadamupeze, adatero iye. +Kadadzera adati chodabwitsa nchakuti apolisi alibe lipoti lokhudza munthu yemwe akuti adasowayo komanso atachita chipikisheni mnyumbamo sadapezemo munthu wosonyeza kuti amasungidwa mobedwa. +Kusanthula ntchito ya fisi Miyambo ya makolo ndi yambiri ndipo ina akuti siyofunika kupitirira chifukwa ikuthandizira kufalitsa kachilombo koyambitsa matenda a Edzi. Sabata yathayi, mafumu adali ndi msonkhano mumzinda wa Lilongwe wokambirana za miyambo. Umodzi mwa miyambo yomwe ikukanidwa ndi mwambo wa fisi omwe ambiri amausokoneza ndi mwambo wa kusasafumbi. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Senior Chief Lukwa wa ku Kasungu pa zamwambowu. Adacheza motere: Lukwa: Mafumu tikuthana ndi miyamboyi Gogo tandimasuleni eti mwambo wa fisi ndi mwambo wanji? Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Pamwambowu munthu amalembedwa ganyu yobereka ana mnyumba ya munthu yemwe zikumukanika. Imakhala ganyu ngati kuti munthu wagula galimoto koma satha kuyendetsa ndiye amalemba munthu yemwe amatha kuyendetsa kuti azimuyendetsera nkumulipira. +Basi? Nanga Fisi uja amalowa mnyumba yoti mwini wake wamwalira kapena asungwana akuchoka kutsimba ndi uti? Choyamba ndikonze kuti amene uja si fisi. Umene uja ndi mwambo wa kuchotsafumbi. Fisi ndi pokhapokha ngati wina akulephera kubereka ana mnyumba ndiye pofuna kuti asachite manyazi mmudzi, amalemba fisi kuti amuberekere mwana kapena ana koma zimakhala zachinsinsi zongodziwa bambo, mayi ndi fisiyo basi. +Nanga kusasafumbi nkutani? Ndikufunatu ndimvetsetse. Kusasafumbi kuli pangapo. Nthawi zina mwamuna akamwalira, mnyumbamo mumabwera mwamuna wina kudzagona ndi mai osiyidwayo akuti kugoneka mzimu wa malemuyo. Nthawi zina mkazi akachotsa pakati kapena anamwali akamachoka kutsimba, amatenga mwamuna woti agonane nawo pokhulupirira kuti kutero ndiye kuti ayendetsa mwambo momwe uyenera kukhalira. +Malipiro ake amakhala chiyani? Zimatengera pangano la awiriwo, ena amatha kulipirana mbuzi kapena nkhuku mwinanso ndalama. Apa palibe dipo lenileni lokhazikika chifukwa nzachinsinsi moti ozidziwa amakhala okhawo okhudzidwa. +Nanga pambuyo pake fisi atatembenuka kuti akufuna ana ake zingathe bwa? Ichi nchibwana chachikulu chifukwa potengera momwe mwambowu umayendera, iye akagwira ntchito pathupi nkuoneka, akangolandira zake basi kwatha zammbuyo muno nza eni nyumbayo. Kuchita masewera, akuluakulu akhoza kugwirapo ntchito chifukwa woteroyo waphwanya mwambo wachinsinsi omwe adavomereza yekha. +Boma ndi mabungwe amati miyambo yotereyi ndi yoipa makamaka nkubwera kwa kachilombo koyambitsa matenda a Edzi, muti bwanji? Zimenezo nzoona zokhazokha moti mafumu kuyambira ku Chitipa mpaka ku Nsanje, Nkhotakota mpaka Mchinji tidagwirizana chimodzi kuti mmadera mwathu miyamboyi isamachitike. Tidachita izi dala chifukwa omwe amazunzika kwambiri ndi amai ndi asungwana chifukwa kumatheka bambo mmodzi kusasafumbi asungwana kapena amai angapo choncho matenda a Edzi sangathe ayi. +Nanga poti mwambo ndi mwambo, mungathe kuwaletseratu anthu? Mfumu siyilephera makamaka pomwe ikutsogolera anthu ake pachinthu chabwino. Monga ndanena kale, mafumu tidamanga fundo imodzi moti kumupeza wina akuchita khalidweli, timamulanga potengera malamulo omwe tidamanga komanso timaonetsetsa kuti onse okhudzidwawo akayesedwe kuchipatala ngati sadavulazane ndi matenda. +Obera malova akuchuluka Akapsala obera achimata amapepala awo powalonjeza ntchito zomwe chikhalirecho palibepo akuchulukirabe mmizinda ngakhale kuti apolisi ndi unduna wa zantchito akulimbana ndi mchitidwewu. +Kumapeto a mwezi wathawu, pa 29 August, apolisi mboma la Mchinji adagwira Yohane Chimkumbi, wa zaka 32, wa mmudzi mwa Ndeleya kwa T/A Mamvere pomuganizira kuti adadya ndalama zokwana K87 000 atanamiza achinyamata 6 kuti awalemba ntchito mbungwe lake, koma adati aliyense ayambe wapereka K10 000. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Wachiwiri kwa mneneri wa apolisi mbomali, Rome Chauluka, adati mkuluyu akuti adauza achinyamatawo kuti pali bungwe lotchedwa Young Advocacy lomwe likufuna anthu oti liwatumize mmadera osiyanasiyana kukagwira ntchito. +Munthuyu adangobwera nkuyamba kuuza achinyamata kuti pali mwayi wa ntchito ndiye mwina ndi ulovawu aliyense akusakasaka mwayi wa ntchito kotero kuti atawauza kuti apereke K10 000 aliyense adangoona ngati mwayi wapezeka, adatero Chauluka. +Akuti amati akamufunsa amanena masitetimenti osiyanasiyana monga oti akungodikira mabwana ake kuti amumasule kulemba achinyamatawo koma ataona kuti payamba kutentha, iye adathawa kuderalo, adatero Chauluka. +Sabata zingapo zapitazo, Tamvani idasokolotsa nkhani ya akamberembere ena omwe amanka mmizinda kukhoma zikalata zoti akufuna achinyamata omwe akusowa ntchito koma atafufuza adapeza kuti nkhani yake idali yomweyi yofuna kuwabera. +Wapampando wa bungwe loyendetsa mabungwe a achinyamata la National Youth Council of Malawi (NYCOM), Aubrey Chibwana adati vutoli lingathe achinyamata atakhala ndi mtima wongogwira ntchito modzipereka ngakhale asadamalize maphunziro awo ndi cholinga choti asadzavutike kupeza ntchito mtsogolo. +Apolisi mbweee! ku PAC Kwa munthu wongofika kumene mumzinda wa Blantyre, ngakhale nzika za mzindawu, sabata imene yangothayi kudali chitetezo chokhwima zedi pomwe apolisi adali ponseponse. Kuyambira mmawa, apolisi adali ndi ma rodibuloku adzidzidzi mmadera ena. +Mmodzi mwa anthu okhala ku Machinjiri, Leston Kampira, Lachitatu adati adadabwa ndi mndandanda wa galimoto umene udalipo pa Wenela. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Tidayenda pangonopang;ono mpaka kukafika pa Wenela kuchoka pa HHI. Tidapeza kuti apolisi amaimitsa galimoto iliyonse ndikuchita chipikisheni kubuti. Ati apolisi amaopa kuti anthu ena apita ndi zida kumsonkhano wa PAC [Public Affairs Committee], adatero iye. +Msonkhano wa bungwe lounikira momwe dziko lino likuyendera la PAC udali kuchitika ku Sunbird Mount Soche ndipo usanayambe mlangizi wa pulezidenti pa zochitika mdziko muno Hetherwick Ntaba adati boma limadziwa kuti pali anthu 300 amene amakonza zipolowe msonkhano wa PAC ukangotha. Msonkhanowo udaliko Lachitatu ndi Lachinayi. +Ndipo Kumbukani Mhlanga wa ku Chinyonga adati adadabwa kuona apolisi akuimika galimoto iliyonse yolowa mtauni. +Zidatichedwetsa ku ntchito. Ndipo ndimadabwa kuti chikuchitika nchiyani ndisanamve kuti kuli msonkhano wa PAC, adatero iye. +Kuchuluka kwa apolisi sikudali mmisewu mokha, ngakhalenso kuhotelayo, apolisi adali mbweee, ena atanyamula mfuti zawo. Pa gulu la apolisi omwe anali ku msonkhanowo, oitanidwa ndi PAC adali 6 okha, malinga ndi mkulu wabungwelo Robert Phiri. +Koma Phiri adati kuonjezereka kwa apolisiwo sikunasokoneze dongosolo lawo chifukwa adakonzekera. +Tidadziwa kuti apolisi abwera ochuluka potengera nkhani zomwe zidamveka za chisokonezo. Mwina nthumwi zina zidasokonezeka, koma ife tachita mmene tidakonzera, adatero Phiri. +Mmodzi mwa nthumwi ku msonkhanowo, mkulu wa bungwe la Peoples Land Organisation (PLO) Vincent Wandale adati anthu adadabwa ndi gululi, koma adamasuka kukamba zotukula dziko. +Zidali ngati dziko likulamulidwa ndi apolisi. Nthumwi zaboma zidabwera zambiri, sitikudziwa kuti amaopa chiyani. Ubwino wake aliyense adapereka mfundo zimene adakonza. Zoopa apolisi zidali kale ndipo sitidanjenjemere kupezeka kwawo, adatero Wandale. +Mneneri wa polisi mdziko muno James Kadadzera adati kuchuluka kwa apolisi sikudali kuopseza anthu koma kupereka chitetezo. +Ndife osangalala kuti msonkhano watha popanda zovuta zili zonse. Timapezeka pofunika chitetezo kuti aliyense agwire ntchito yake mosaphwanya lamulo osati kuopseza. Ndipo okonda dziko lake sanganene kuti apolisi adalakwitsa, adatero Kadadzera. +Chitetezo chapolisi chokhwimachi chidaonekeranso pamene apolisi mogwirizana ndi khonsolo ya mzinda wa Blantyre adaphwanya ndi kulanda makontena amene anthu amachitiramo bizinesi mumzindawo. Izi zidachitika usiku wa Lolemba ndi Lachiwiri. +Sitilembetsa mayeso Aphunzitsi amene alembetse mayeso a Fomu 4 a chaka chino omwe ayambe pa 22 June, aopseza kuti sadzagwira ntchitoyo ngati Unduna wa Maphunziro salandira ndalama zomwe amapatsidwa akamapita kutchuthi. +Izi zikudza pamene ophunzira ndi makolo ena msukulu za pulaimale akudandaula kuti sitalaka ya aphunzitsi isokoneza kukonzekera mayeso a temu yachitatu omwe ayambe kumayambiriro kwa mwezi wa July. Aphunzitsi pafupifupi 63 000 akuchita sitalaka pofuna kukakamiza boma kuti liwapatse ndalama zomwe amalandira akamapita kutchuthi za chaka cha boma cha 2016-2017 chomwe chithe pa 30 June. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Apolisi adathamangitsa ana ku Chileka Tamvani wapeza kuti pambali pa sitalaka imene yachititsanso kuti ana a sukulu za pulaimale zina apite pamsewu kudandaula kuti sakuphunzira, zokonzekera mayeso a Fomu 4 zili gwedegwede chifukwa kusamvana pakati pa boma ndi aphunzitsi kukupitirira. +Mlembi wa Teachers Union of Malawi (TUM) Charles Kumchenga adati palibe mphunzitsi alembetse mayeso msukulu komanso kuyanganira mayeso a MSCE asadalandire ndalama ya tchuthi pachaka. +Boma limayenera kusamalira umoyo wa oyanganira mayeso omwe ndi aphunzitsi. Ophunzira akulangika chifukwa cha kholo lathu, boma. Boma lidalemba ntchito mphunzitsi kuti asamalire ana kumidzi ndipo lili ndi mayankho pa mavuto onsewa, iye adatero. +Naye mkulu wa TUM, Willie Malimba, adati aphunzitsi ndi okhumudwa chifukwa boma ndi onse okhudzidwa akukanirana zofuna zawo. +Iye adati boma lingopereka ndalamazi osati kumangoyankhula zomwe zina zikulowa mabodza. +Bungweli lati lipereka chenjezo ku boma ndi nthambi ya mayeso ya Malawi National Examination Board (Maneb) kuti palibe mphunzitsi ayanganire mayeso asadalandirenso ndalama ya ntchitoyi. +Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a za maphunziro mdziko muno la Civil Society Education Coalition (CSEC) Benedicto Kondowe wati mayeso a MSCE akhoza kupepuka malinga ndi zomwe zikuchitikazi. +Kukhumudwa komwe kulipo kudzetsa kubera mayeso. Choopsa chichitika pa maphunziro mdziko muno ngati sitisamala. Kulemba kwa mayeso a gawo lachitatu msukulu za pulaimale mu July nkosathandiza chifukwa umafunsa zomwe waphunzitsa ndipo apa ana sakuphunzira. Tisaiwalenso kuti awa ndi mayeso woti ana apite kalasi ina, iye adatero. +Iye adati ndi wokhumudwa ndi kulekerera kwa boma pa nkhani ya ndalama ya tchuthiyi ndi mavuto ena aphunzitsi omwe likuyenera kukonza. +Boma silimvera zokhumba za aphunzitsi ndipo avutika kwa nthawi yaitali. Nthawi yakwana yokakamiza boma kupereka zomwe ndi zawo. Kuti boma lilimbikitse maphunziro abwino, makolo alimbe mtima kulifunsa chifukwa chomwe ana awo sakuphunzira ndiponso ana achite zomwezo, adatero Kondowe. +Msabatayi, aphunzitsi adalowa sabata yachiwiri akuchita sitalaka ndipo ana nawo adalowerera sitalakayo. Ana ophunzira msukulu zina ku Blantyre, Ntcheu ndi Balaka adapita pamsewu kuyambira Lolemba pofuna kukakamiza boma kumva kulira kwa aphunzitsi awo. +Pambali potseka misewu ina, ana enanso adamenya ndi kuvulaza apolisi atatu ku Lunzu mumzinda wa Blantyre, pomwe anthu 23 kuphatikizapo ophunzira 9 adamangidwa ku Ntcheu. Apolisi adathamangitsa ana ku Ndirande ndi utsi okhetsa misozi. +Kafukufuku wa Tamvani adasonyeza kuti ana mmaboma ambiri mdziko muno sakuphunzira. Ana ndi aphunzitsi ena sakupita ndi kusukulu komwe. +Mwachitsanzo, pasukulu ya pulaimale ndi sekondale ya Katoto mumzinda wa Mzuzu, tidapeza ana ali khumakhuma kulingalira za tsogolo lawo. Ena adali kusewera mpira. +Sindkuona bwino za kutsogoloku. Tikawafunsa aphunzitsi sitalaka itha liti, akutiyankha kuti sakudziwa, si zili mmanja mwawo. Ena a chifundo akumatiphunzitsa nthawi zina, adatero wophunzira wa Fomu 2. +Richard Mbulu: Chilombo cha Mafco FC Dzina la Richard Mbulu lasanduka nyimbo ya mizinda yonse chifukwa cha ntchito zake zomwetsa zigoli. Pano Mbulu akutsogola mu TNM Super League ndi zigoli 11, adamwetsanso zigoli 17 mu Presidential Cup. Kodi Mbulu ndani? BOBBY KABANGO akucheza naye. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mbulu: Chilombo pankhani yokankha chikopa Wawa Mbulu Mbuluyo ndiye ineyo, mani. +Kodi ndi Mimbulu? Kapena Mbulu basi? Ndine Mbulu, koma dzina limeneli likuchokera ku dzina loti Mimbulu, tinyama tovuta kwabasi. +Ndiye iwe ndiwe wovuta? Kumbali ya mpira basi, kuvuta kwanga ndi kumeneko, koma zinazi ndiye ndine munthu wabwinobwino. +Timudziwe kuti Mbulu ndani? Mbulu ndi ineyo, mnyamata wochokera ku Mangochi, woyamba kubadwa mbanja la ana asanu. +Mbiri yako pachikopa ndiyotani? Poyamba ndimasewera ku Navy FC kapena kuti Marine MDF, nditachoka kumeneko, ndidakatera ku [Big] Bullets komwe ndidakhalako kwa miyezi iwiri. Ku Navy ndidachokako nditangolemba mayeso a Form 4 mu 2013. +Zidayenda bwanji ku Bullets? Sadandipatse mwayi woti ndisewerere mtimuyo, panthawiyo amati ndine mwana. Ndidachoka ulendo ku Mafco FC komwe adandilandira bwino. +Chipitireni ku Mafco wachinya zingati? Ndachinya zigoli 108 za ligi ndi makapu omwe, apatu ndikutanthauza kuyambira 2013 mpaka lero. +Mphekesera zikuti mwayi wapezeka wokasewera ku Baroka FC ku Joni, ndi zoona? Zili choncho koma sindingayankhe zambiri pankhaniyi. Ineyo ndine msirikali ndiye oyenera kuyankha pankhani imeneyi ndi mabwana anga. +Anatchereza Wokondedwa Anatchereza, Zikomo chifukwa cha malangizo amene mukumapereka. Thandizeni. +Ndili ndi mkazi yemwe ndakhala naye kwa nthawi ndithu. Iye adapezeka wodwala ndipo mthunzi wake utatsala miyezi iwiri kuti akhale ndi mwana, makolo ake adamuitanitsa. Pozindikira kuti izi zimachitika, ndidaloleza kuti apite. +Ndipo sindidafowoke kumuthandiza nthawi yonseyo mpaka kuchira. Koma atachira, achibalewo adati ndichoke kumene ndikukhala ndipite kwawoko. +Sindidagwirizane nazo ndipo ndidakana. Mwanayo atabadwa, adati ndisapite kukamutenga koma ndipite komweko tizikakhala. Sindidagwirizane nazo ndipo ndidaneneratu kuti sindingapiteko. +Lero patha miyezi 13, ndipo makolowo akunena kuti ndipite kumudziko ndikamutenge mwanayo. Ndichitenji? SL, Balaka SL, Zikomo chifukwa chondikhulupirira. Choyamba mukuyenera kuzindikira kuti pena anthu amakhala ndi zikhulupiriro zosiyanasiyana. Ndikulangizani molingana ndi kuti simunatiuze ngati mkazi wanu ndi inu muli a mitundu yofanana. +Ngati muli a mtundu umodzi, mukudziwa chimene ndikunena. Komanso mukuyenera kudziwa chimene makolowo akuchitira izi. +Nchifukwa chake ndinganene kuti ngati muli a mtundu umodzi, mwina mukhoza kudziwa kuti panali china chimene amafuna achite naye mwanayo, ndiye amakumangani. Koma chifukwa sizinatheke, nchifukwa akukuuzani mupite. +Koma zonsezo ndi inu ndi mkazi wanu. Kodi maganizo ake ali pati? Akudziwa, akuuzani. +Sindikhulupirira zaufiti, koma izitu ziliko. +Tsono pa ganizo lakuti mukamutenge mwanayo kapena ayi, ndikuuzani motere: mwanayo mukamutenge, chifukwa ndi wanu. Koma mupite kukamutenga patapita nthawi mpaka kutamvetsetsa chimene chikuchitika. Pitirizani kumuthandiza kuti musamuphere ufulu. +Cholinga choti pathe nthawi kaye nchakuti, muone momwe zikukhalira. Panopa, tumizani zofunika. +Anatchereza. +Kodi akazi amafuna chiyani? Zikomo Anatchereza, Ine ndi mnyamata wa zaka 24 ndipo ndikusaka msungwana wakuti ndimange naye banja. Komatu zikundivuta. +Vuto lalikulu ndilakuti sindikudziwa kuti akaziwa amafuna chiyani kwenikweni. +Izitu ndikunena chifukwa cha zomwe ndakhala ndikuziona. Panopa ndafunsira akazi okwana atatu koma chomwe ndikuchiona nchakuti ngakhale akundikana, pakatha masiku angapo, amandiimbira, kapena kuchita zina, kundikopa kuti chibwenzi chiyambepo. +Nchifukwa chiyani akuchita izi? Ndikufuna kukwatira, koma sindikudziwa kuti kwenikweni amafuna chiyani? Thandizeni gogo. +CGS, Karonga CGS, Zikomo chifukwa cha uthenga wanu. +Mkazi asanalole mwamuna ukwati, amadikira kaye ngatidi mwamunayo watsimikiza. +Akatero, amaona kaye ngati mwamunayo angamuthandize. Apa amaunikiranso ngati angayanjane magazi polingalira mtundu, chipembedzo, maphunziro ndi zina zotero. +Malingaliro otero angabweee patatha nthawi tsono nchifukwa chake kuyambira kale amanena kuti ndikuyankha mawa. +Iyi imakhala nthawi yoti akufufuzeni ngati simukudziwana bwino. +Kodi inuyo mbiri yanu njotani? Mwinatu akaziwo sakukudziwani ndiye akafufuza akupeza kuti mulibe banga, nchifukwa chake akubwerera kuti mukwatirane nawo. +Malangizo anga ndi akuyi, musanafunsire, muzimulola mkaziyo akudziweni. Muzimupatsa nthawi yokwanira ndi kumulola kuti akudziweni bwinobwino. +Kupanda kutero, palibe chotheka. +Anatchereza. +Dzombe kukoma, koma Kuyambira makedzana, panthawi ya ulendo wa ana Aisiraele kuchoka ku Aigupto kupita kudziko lolonjezedwa lija la Kenani ngakhalenso nthawi ya Yohave Mbatizi anthu akhala akudya dzombe, chiwala chomwe ambiri amachitama kuti chilibe chinzake kumbali ya makomedwe. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ku Malawi kuno dzombe si lachilendo ndipo anthu akhala akusimba za kandiwo koutsa mudyoka. +Ngakhale mdziko mukagwa dzombe limaononga mmera mminda ndi zomera zina, kumbali ina amakhala madalitso chifukwa ngati ndiwo, zoulukazi zilinso ndi ubwino wake kuthupi la munthu chifukwa zili ndi ma protein ochuluka komanso zinc ndi iron, michere yomwe imathandiza kumanga thupi, malingana ndi kafukufuku wa bungwe la Food and Agriculture Organisation (FAO). +Ngakhale pali chiletso, dzombe likugulitsidwa malicheromalichero mmisika monga ku Limbe ndi ku Blantyre Mmene zidamveka pa July 22 chaka chino, kuti dzombe latera kusikimu ya Nyamula mboma la Nsanje ndipo likukhamukira ku Bangula mpaka lafika ku Chikwawa, odziwa za kukoma kwa ziwala zosowazi adangoti laponda lamphawi-ndiwo zapezeka! Ndi njala ndi njala yomwe yabonga mmaboma awiriwa ambiri sakadatha kuchitira mwina koma kuthokoza Mulungu chifukwa chowatumizira dzombe kuti akhwasule. Nanji kuti lambiri limapezeka lofooka komanso lina lofa kale! Mauthenga ochenjeza anthu kuti asabwekere dzombeli chifukwa lapoperedwa mankhwala kuti lisapitirize kuononga mmera kuchigwa cha Shire, koma ena akhala akunyalanyaza ndipo sakusiya kutola ndi kukazinga dzombeli nkumadya mtima uli mmalo. +Senior Chief Malemia wa mboma la Nsanje komanso mtsogoleri wa komiti yokhazikitsa chitetezo mboma la Chikwawa, Mike Kalula, atsimikizira Msangulutso za nkhaniyi. +Uthenga wafika paliponse kuti tisadye dzombeli chifukwa alipopera mankhwala. Koma ena akumatolabe nkulitsuka kenaka akukulidya. Ndi zoopsa kwambiri, komabe tikuyesetsa kuwalangiza kuti asiye kudya dzombeli, adatero Kalula. +Vuto la kuno ndi njala. Kuli njala yadzaoneni ndiye anthu sangapirire kuti asadye dzombeli pamene alibe podalira, komabe sakuyenera kutero. Ndi bwino kufa ndi njala kusiyana kufa ndi mankhwala. +Naye Malemia akuti nkhaniyi yawadzidzimutsa ndipo apempha kuti anthu asiye kudya dzombe lofa ndi mankhwala. +Malipoti oti anthu akumatsuka dzombeli ndi kudya atipezadi, ndipo tili ndi mantha chifukwa titha kutaya miyoyo ya anthu, adatero Malemia. +Iye adati kutsatira chiletso cha boma, mboma la Nsanje anthu aleka kugulitsa dzombeli komabe ena akugulitsabe mobisa. +Chinthu chikaletsedwa, palibe amene angagulitsire poyera, nkutheka ena akugulitsa mobisa koma ndikuti ayenera kusiya mchitidwewu chifukwa avulaza anthu, adatero. +Mlembi wamkulu muunduna wa zamalimidwe, Erica Maganga, wati wakhumudwa ndi nkhaniyi ndipo wapempha anthu kuti alekeretu kudya dzombeli ponena kuti zingathe kuika miyoyo yawo pachiopsezo. +Awanso ndiye mavuto enatu, ife taletsa kuti anthu asadye dzombeli chifukwa angathe kukumana ndi mavuto. Ngati boma lalankhula ndiye kuti laonapo kuipa komwe anthu angakumane nako akadya dzombe lofa ndi mankhwala oopsa. +Atha kudya mwina osaona kukhudzidwa kwake, koma izi zingathe kuwakhudza patsogolo, kotero akuyenera kusiya. Tipemphe amabungwe, atolankhani ndi ifeyo kufalitsa uthengawu kuti anthu asaononge dala miyoyo yawo chifukwa chosusukira dzombe, adatero Maganga. +Iye adati chiletso chosadya dzombe ndi ziwala chakhudza maboma a kuchigawo cha kummwera chifukwa ndiko kwayandikira maboma a Chikwawa ndi Nsanje amene akhudzidwa ndi kugwa kwa dzombeli. +Vuto ndi loti ndi zinthu zouluka, ndiye pena uzipeza zafika ku Thambani mpaka kukalowa mboma la Neno lomwe layandikana ndi maboma amene akhudzidwawa. Ndiye tikuti maboma onse kuchigawo cha kummwera asadye ziwalazi. Tikugwira ntchito ndi apolisi kuti asapezeke wina akugulitsa dzombe kapena ziwala, adaonjeza Maganga. +Dotolo wina amene adati tisamutchule dzina chifukwa sayankhulira unduna wa zaumoyo, wati anthuwa ali pachiopsezo ngati akudyadi dzombeli. +Pali mavuto oti angathe kumachita chizungulire, kumva zoyabwa mthupi komanso kutentha thupi chifukwa cha mphamvu ya mankhwalawa, adatero poyankhapo zomwe zingawachitikire anthu amene adya dzombe lopoperedwali. +Mkulu woyanganira za mbewu ku Shire Valley ADD, Ringstone Taibu wati mahekitala ambiri athiridwa mankhwala ndipo ntchito yachitika kwa sabata zitatu. +Kupatula kusasantha mmera wa alimi, dzombeli lidadyanso nzimbe kuminda ya kampani ya Illovo zomwe zidachititsa kuti alipopere mankhwala. +Anatchezera Za Chikondi ndi chibwenzi Agogo, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kodi chibwenzi ndi chikondi ndi zosiyana bwanji? Mwina funso limeneli likhoza kuoneka ngati lopanda nzeru koma kwa ine ndi lofunika kwambiri. Funso lina ndi loti kodi ngati mwamuna amakonda kulonjeza chibwenzi kapena wachikondi kuti adzakwatirana chonsecho mkazi samamulonjeza mwamuna wake, ndiye pamenepa mwamuna angathe kupitiriza chibwenzi kapena angomusiya? LF, Area 12, Lilongwe Wokondeka LF, Munthu utha kukhala ndi abwenzi ambirimbiri koma wachikondi mmodzi. Nthawi zambiri anthu satha kusiyanitsa pakati pa chikondi ndi chibwenzi. Chikondi ndi chozama kuposa chibwenzi; chikondi chimachoka pansi pa mtima ndipo nthawi zambiri anthu awiri akakondana maka pakati pa mwamuna ndi mkazi amagwirizana mzambiri moti nchifukwa chake mapeto ake amalolerana ndi kulumbira kuti adzakhala limodzi mpaka moyo wawo wonse mbanja, pamene chibwenzi mumatha kugwirizana pa zina koma kusiyana mzambiri zochitika. Nchifukwa chake munthu utha kukhala ndi abwenzi ambiri ngakhale uli pabanja, monga ndanena kale, koma amene umatherana naye nkhazi zakukhosi ndi zakumphasa ndi mmodzi yekha, wachikondi wako. Funso lako lachiwiri yankho ndi loti pachikhalidwe chathu mwamuna ndiye amafunsira mkazi ndipo ndi iyeyo amene amauza mkazi za cholinga chake pachibwenzi chawocho. Akazi ambiri amakhala ndi manyazi kunena kuti alola chibwenzi chonsecho mkati mwa mtima wawo alola kale. Ndiye munthu wamwamuna uyenera kumvetsa ndi kufatsa; osapupuluma chifukwa ukhoza kutsekereza mafulufute kuuna poganiza kuti mkazi sakunena chilichonse. Pamene pali chikondi sipasowa, zochitika zimasonyeza zokha kuti apa pali chikondi ngakhale wina asanene. +Ziphuphu mkalembera Pamene kalembera wa unzika za dziko lino ali mkati, zadziwika kuti anthu ena apeza mpata wosolola mmatumba mwa Amalawi omwe akutenga nawo gawo lolembetsa mukalemberayu. +Amalawi ena akumafunsidwa kupereka K500 kapena kuposera apo kuti apeze mwai wa fomu yolembapo mbiri yawo. Izi zikumachitika makamaka pamalo akalemberayu pakakhala khwimbi la anthu omwe akumauzidwa kuti mafomu atha ndipo apereke kangachepe kuti ziwayendere. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mwachitsanzo, Lachiwiri lapitali apolisi mboma la Dowa adatsekera ofesala wa bungwe lomwe likuyendetsa kalemberayu la National Registration Bureau(NRB) yemwe amayanganira ntchitoyu pa malo akalembera a Chuzu, kwa Traditional Authority(T/A) Nkukula mbomalo pomuganizira kuti amalandira ziphuphu. +Ena mwa anthu omwe amalembetsa pamalopa amauzidwa kuti mafomuwa atha ndipo apitenso tsiku lotsatira ndi K500, ndipo mafomuwa akumatulukadi. +T/A Nkukula adavomereza kuti apolisi atsekeranso munthu wina yemwe adapita pa malo a Chuzu ndi kutenga mafomu atatu ponena kuti ena ndi a abale ake kunyumba koma amatsatsa mafomuwo pa mtengo wa K500. +Komanso masiku apitawo chifukwa cha mitambo makina a kalemberayu adalibe moto choncho anthu ena adasonkha ma K200 nkukagula maunitsi a magetsi omwe adatchajira makinawa kuti zinthu ziyende, adatero Nkukula. +Komatu si ku Dowa kokha chifukwa nako ku Dedza ziphuphu zikuperekedwa kuti anthu ena apeze mwai olembetsa nawo mkalemberayu. +Malinga ndi mzimai wina wochokera pa malo a kalembera a Katsekaminga yemwe adapempha kuti tisamutchule dzina lake, adapereka K500 kwa mfumu ina mderali kuti apeze mwai wa fomu yolembapo mbiri yake. Polankhulapo T/A Kamenyagwaza wa mboma la Dedza adati ngakhale kalemberayu wayenda bwino mmalo ena, vuto lalikulu lili pamalo a kalembera a Bembeke pomwe anthu akuvutika kuti apeze mafomu. +Anthu ozungulira pa Bembeke akumauzidwa kuti mafomu atha ndipo akumakapempha pamalo ena a Liberito komwe mphekesera yandipeza yoti akumawatchaja kangachepe, adatero Kamenyagwaza. +Ndipo mneneri wa bungwe loyanganira kalemberayu Norman Fulatira adavomereza zoti bungweli lalandira madandaulo a ziphuphu mmalo ena. Tikupempha Amalawi akufuna kwabwino kuti azititsina khutu za mchitidwewu ndipo ife mogwirizana ndi apolisi tidzachita kafukufuku, adatero Fulatira. +Iye adatsimikizanso za kutsekeredwa kwa ofesala wawo wa pamalo a kalembera a Chuzu. +Ntchito ya kalembera wa unzika idayamba mwezi wa May ndi cholinga chofuna kuti mwazina nzika za maiko ena zisamalandire nawo thandizo lopita kwa Amalawi monga mzipatala zomwe zili mmalire a dziko lino ndi maiko ena. +Minibasi zikwera Mwachinunu Nthawi zonse minibasi zikamakweza mtengo, makamaka mafuta akakwera, bungwe la eni minibasi limalengeza, ndi kuika mitengo ya minibasi kuti aliyense adziwe. Koma kuchokera Loweruka lapitalo, mitengo ya minibasi mmadera ena idakwera mwachinunu. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Izi zidachitika patangotha tsiku limodzi kuchokera pomwe oyendetsa minibasi adanyanyala ntchito zawo ati pokwiya ndi zilango zina zimene amalandira akaphwanya malamulo a pamsewu. +Amalawi amene tacheza nawo ku Blantyre, Lilongwe ndi Mzuzu adati ndiokhudzidwa ndi kukwezaku, komwe cholinga chake sichikumveka. +Mandiya: Okwera akuyenera kupereka yochuluka basi Mmodzi mwa anthu omwe akhudzidwa ndi mitengoyi, Sydney Chingamba wa ku Chilomoni yemwe amagwira ntchito ku Ginnery Corner mumzinda wa Blantyre, wati ichi ndi chitonzo ndipo okwera akuyenera kuchitapo kanthu kuti mitengo ibwerere. +Kafukufuku wa Msangulutso wapeza kuti mitengoyi yakwera ndi K50 kapena K100 mmadera osiyanasiyana mmizindayo. +Malingana ndi mmodzi mwa madalaivalawa mu Limbe, Fatchi Madani, iyi ndi njira yoti galimoto itulutse ndalama zomwe eni minibasi amafuna patsiku ngakhale pali malamulo okhwimawa. +Okwera akuyenera kupereka ndalama yochuluka basi. Patsiku bwana amafuna K10 000 ndipo kutenga atatu pampando pa K500 kukawasiya kwa Goliati ndi phada ameneyo. Ngakhale tisatenge anayi-anayi pampando ndalama izipezeka yokwanira chifukwa cha mitengoyi, adatero Madani. +Naye Phillip Bwanali, woyendetsa galimoto pakati pa Limbe ndi Blantyre, adati akweza mitengo chifukwa sakuloledwa kunyamula katundu [chimanga, mtedza ndi zina] yemwe okwera amamulipira mwa padera. +Tatero kuti tisavutike ndi kupewa ena kuyamba kuba ndi umbanda. Mmene chilili chuma cha dziko lino anthu ambiri sangakwanitse kutenga katundu pa matola omwe ndi okwera mtengo kusiyana ndi maminibasi, iye adatero. +Poyankhapo, mkulu wa bungwe la eni minibasi la Minibus Owners Association of Malawi (Moam), Coaxley Kamange adati ndi odabwa ndi zimenezi ndipo wangomva mphekesera kuti madalaivala achita moteremu. +Izi sizikutikhudza. Aliyense akhoza kuchita chili chonse ndi mitengo chifukwa lamulo likulola anthu kutero. Takhala tikudzudzulidwa ndi bungwe la Competition and Fair Trading Commission (CFTC) pamene timakonza mitengo mmbuyomu ndipo tidasiya, adatero Kamange. +Iye adati izi ndi zosokoneza anthu chifukwa akudziwa zakusinthaku ali mminibasi kapena padepoti. +Timayenera kutenga gawo pa chiganizochi kuphatikizapo okwera kuti mitengo ikhale yokomera onse. Bungweli [CFTC] lidati tisamakonze mitengo ya minibasi, koma padakalipano ndondomeko yabwino palibe, adatero Kamange. +Mkulu wa bungwe loona ufulu wa okwera la Passengers Welfare Association of Malawi (Pawa), Don Napuwa, adati izi ndi zokhumudwitsa ndipo madalaivala sakuyenera kukweza mitengo ya galimoto chifukwa boma langokhwimitsa ndi kuyamba kutsatsa malamulo omwe adalipo kale. +Madalaivala akusokoneza. Ngakhale kunyanyala ntchito komwe adachita sabata yatha eni galimoto sadadziwitsidwe. Mitengoyi imakwera potengera mtengo wa mafuta ndipo mafuta sanakwere. Oyendetsawa alibe danga lokweza mitengo, adatero Napuwa. +Tidagwirizira ukwati wa mnzathu Akuti wokaona nyanja adakaona ndi mvuu zomwe. Naye wokagwirizira ukwati wa mnzake, adakapezako banja. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Izitu zikupherezera pa wolemba nkhani wa Times Group ku Mzuzu, Sam Kalimira, yemwe adakumana ndi bwenzi lake Chisomo Makupe pogwirizira ukwati wa mnzawo. +Awiriwa adavinira limodzi paukwatiwo. +Udali mwezi wa August, mchaka cha 2014, pomwe Kalimira adamuona koyamba Chisomo patchalitchi cha CCAP cha Mchengautuwa mumzinda wa Mzuzu. +Monga achitira atsikana ambiri, Chisomo adali pakagulu ka atsikana anzake. Chisomoyutu adali atachokera ku Lilongwe komwe amakhala kudzagwirizira ukwatiwu. +Ngakhale akuti adalibe maganizo omufunsira, koma pansi pamtima adayamikira ndithu kuti namwaliyu ndi mkazi wabwino. +Ndikulonjeza: Sam kuveka mphete Chisomo patsiku la chinkhoswe chawo Nditangomuona, mumtima mwanga ndidadziuza kuti namwaliyu ndi mkazi wabwino ngakhale ndidalibe ganizo loti ndingamufunsire ndipo tsiku lina nkudzaganiza zomanga naye banja, adatero Sam. +Mwina tingati, mtima wa mnyamayu sudasunthe kwenikweni chifukwa panthawiyo adali ali ndi bwenzi lina lomwe ankalifera. +Koma poti mtima wa mnzako ndi tsidya lina, ubwenziwu udatha ndipo Sam adakhala kwa miyezi yokwana 8 opanda bwenzi. +Apatu adali akulingalira zina ndi zina za moyo maka pankhani zachikondi. Monga mukudziwa kuti nkhani zachikondi ndi zovuta. +Ndidayambanso kulingalira zopeza mkazi womanga naye banja, ndipo mwachisomo cha Mulungu maganizo a Chisomo adandibwerera, adatero Kalimira. +Apa ndi pomwe mwana wammuna nzeru zidamuthera chifukwa adali atapanga ubale wa pachilongo ndi Chisomo. +Kalimira adalongosolera Msangulutso kuti awiriwa ankaitanana kuti achimwene ndi achemwali. +Komabe monga mphongo, Sam adachita zotheka kuthetsa zachilongozo ndi kumufunsira namwaliyo. +Tsoka ilo, adakanidwa. +Komabe nditayesayesa mwawi adandilola ndipo chibwenzi chidayamba mwezi wa August 2015, adalongosola motero Kalimira. +Awiriwa sadachedwetsenso koma kupangiratu mwambo wa chinkhonswe nkuyamba kukonzekera zomanga banja. +Wachiona ndani mu tnm Mpikisano wolimbirana ukulu mu 2016 TNM Super League wafika pamponda chimerapalibe amene akudziwikiratu kuti ndiye atenge mapointi ochuluka mligiyi. +Chaka chino zinthu zasiyana ndi zaka zina mmbuyomu. Monga chaka chatha, mmene kudatsala magemu 8 oti matimu asewere, aliyense adali atadziwa kale kuti Nyasa Big Bullets ndiyo itenge ligiyo. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Za chaka chino ndi zina, kwatsala magemu atatu kuti ligiyi ithe, komabe wotenga sakudziwika ngakhale kuti Kamuzu Barracks ndi Bullets akuoneka kuti ali ndi mwayi waukulu. +Umu ndi momwe ilili ligiyi. Matimu asanuKB, Bullets, Blue Eagles, Silver Strikers komanso Mafco FCndiwo ali ndi mwayi wotenga ligiyi. +Bullets (malaya ofiira) kusewera ndi KB mmbuyomu KB ili pamwamba ndi mapointi 52 pamene yasewera magemu 27. Timuyi yatsala ndi magemu atatu amene isewere ndi Dwangwa, Karonga ndi Eagles. Magemu onsewa, KB isewera koyenda. +Bullets, yomwe ikutsatira KB ndi mapointi 51 yaseweranso magemu 27. Iwo ndi omwe akuteteza chikhochi ndipo atsalanso ndi magemu atatu ndi Dwangwa, Civo ndi Eagles. Masewero onse akusewera pakhomo. +Eagles ili panambala 3 ndi mapointinso 51 itasewera magemu 27. Timuyi yatsala ndi magemu atatu ndi KB, Bullets komanso Mafco. Magemu awiri isewera pakhomo. +Achinayi ndi Silver ndi mapointi 50 nayonso itasewera magemu 27. Yatsala ndi Karonga, Wanderers ndi Mafco. Magemu awiri isewera pakhomo. +Pambuyo pa Silver pali Mafco ndi mapointi 47 mmagemu 27 ndipo yatsala ndi Eagles, Civo ndi Silver. Magemu awiri ali koyenda. +Ngati Bullets ingalondoloze mbiri yawo yosagonja pakhomo, ndiye kuti timuyi ili ndi mwayi wotenganso chikho cha ligiyi ngati ingadzagwetse Eagles, Dwangwa komanso Civo. +Komabe izi zingavutireko chifukwa Civo ndi Dwanga akumenya mpira woti asatuluke mligiyi komanso ikukumana ndi Eagles yomwe ikufuna kutenga ligiyi koyamba mmbiri yawo. +Mwayi wa KB ndi wovutira chifukwa timuyi ili ndi mbiri yoipa kusewera kwa eni. Magemu atatu onse ikusewera koyenda, zomwe zikukaikitsa ngati ingakapambane onse. +Eagles ilinso ndi ntchito yovuta chifukwa ikuyenda kukakumana ndi Bullets pakwawo pamene simagonjapo komanso ikulandira matimu akuluakulu, Mafco ndi KB. +Silver ilinso ndi mwayi wotenga ligiyi chifukwa ikumenya ndi Karonga pakhomo pomwe ingapambane koma nkhondo ili pamene ikubwera pa Kamuzu Stadium kudzakumana ndi Manoma. +Koma kochi wa KB, Billy Phambala, akuti KB ndiyo itenge ligiyi chifukwa ili ndi njala yaikulu yonyamula chikho itakwapulidwa mndime yomaliza ya chikho cha Fisd. +Magemu atatu amene tatsala nawo ndi osadetsa nkhawa, tikapambana ndi kutenga ligi, iye adatero. +Akudyerera obwela A malawi akhala akuingidwa ngati nkhuku mmaiko ena akafuna thandizo la chipatala, koma nzika zakunja kumadzawamwera mazira zikafika mdziko muno ponama kuti ndi nzika za dziko lino. +Izitu zakhala zikuchitika chifukwa chosowa chiphaso cha unzika, koma lero mpumulo wafika kwa Amalawi pamene akhale ndi mwayi wokhala ndi chiphaso chosonyeza unzika wa dziko lino. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kuthithikana mzipatala zina kumadza chifukwa cha anthu a kunja Zili chonchi malinga ndi ntchito yomwe bungwe la National Registration Bureau (NRB) poyamba kalembera wa unzika amene adayamba ndi akuluakulu aboma komanso maboma 11. +Monga akufotokozera Senior Chief Kanduku wa mboma la Mwanza, boma lake limalandira nzika zambiri kuchokera mdziko la Mozambique. +Anthu pafupifupi atatu mwa 10 alionse amene amafuna thandizo lachipatala kuno amakhala a ku Mozambique. Vuto ndiloti kuyambira pa Zobue mpaka ku Tete mdziko la Mozambique palibe chipatala, posowa kolowera, anthu adera limeneli amathandizidwa mzipatala za dziko la Malawi, adatero Kanduku. +Ngakhale tayandikana ndi dzikolo, satilola kupita mdziko lawo kukalandira thandizo la chipatala. Amalawi angapo akhala akuthamangitsidwa, ndipo suthandizidwa chifukwa anzathuwo ali ndi zitupa za unzika, adaonjeza motero. +Naye Senior Chief Kabunduli ya mboma la Nkhata Bay, adati kumeneko nzika za maiko a Tanzania zimalowa pafupifupi tsiku lililonse ndi kumalandira thandizo lomwe Amalawi amayenera kulandira. +Akafika kuno amakhala ndi maina a Chimalawi zomwe ndizovuta kuwakaikira kuti si nzika zathu. Mankhwala pachipatala amatha mwachangu ife ndi kumavutika pamene iwo kwawo ali ndi zipatala zomwe zingawathandize, adatero Kabunduli. +Kungofika pa Chintheche pali anthu ambiri amaiko a Burundi, sangapitenso kwawo ndipo akulandira chithandizo chilichonse chomwe chimayenera chipite kwa Amalawi. Kwawo sungayerekeze kupanga zimenezi koma ifeyo amationa kupusa, adaonjeza Kabunduli. +Kuti munthu ulandire thandizo lachipatala cha boma mmaiko monga Zambia, Zimbabwe, Mozambique ndi Tanzania, umayenera kuonetsa chitupa chosonyeza kuti ndiwe nzika koma kuno kwathu izi sizichitika chifukwa kulibe ziphasozi. +Monga akufotokozera Norman Fulatira yemwe ndi mneneri wa NRB, iyi mwina nkukhala mbiri yakale chifukwa Mmalawi weniweni azidziwika ndi chiphaso chomwe adulitse. +Mavuto amenewa akhala mbiri yakale posakhalitsapa pamene ntchito yodula ziphaso za unzika yayamba. Gawo loyamba tayamba kupanga ziphaso za aphungu a Nyumba ya Malamulo, akuluakulu mboma, komanso midzi 27 mmaboma 11, adatero Fulatila. +Mabomawa ndi Chitipa, Mzimba, Nkhotakota, Lilongwe, Salima, Dowa, Mchinji, Blantyre, Mangochi, Chikwawa ndi Thyolo. Zitupazo azidula mmidzi iwiri pa boma lililonse. +Ili ndi gawo loyamba, gawoli likufuna lingotithandiza momwe ntchito ikhalire, ili ngati ntchito yoyeserera kaye koma anthu alandira ziphaso zawo. Mudzi ulionse takonza zoyamba ndi anthu 200 ndipo gawoli likamatha, anthu 5 000 akhala ndi ziphaso zawo, adatero mneneriyu. +Iye adati gawo lachiwiri la ntchitoyi, anthu 95 000 ndiwo adzakhale ndi mwayi wokhala ndi ziphasozi ndipo gawoli likuyembekezereka kudzatha mu December chaka chino. +Chaka chamawa, bungweli likuyembekezera kuti ntchitoyi idzafalikira dziko lonse pomwe anthu 9 miliyoni akuyembekezeka kulandira zitupa zawo. +Fulatira adati aliyense amene wakwanitsa zaka 15 ndiye akuyenera kudulitsa ziphasozi. Iye watinso ngati uli nzika ya dziko lino, uyenera kudulitsa ziphasozi posatengera zikhulupiriro zako kapena mpingo. +Naye mkulu wa bungwe loona zaumoyo la Malawi Health Equity Network (Mhen) George Jobe wati ntchitoyi ipindulira Amalawi komanso boma. +Apapa ndiye kuti thandizo la mabungwe ndi boma lizipitadi mmanja mwa Amalawi enieni kusiyana ndi poyamba pamene timaphangirana ndi obwera, adatero. +Kwa amene ataye chiphasochi akuti ayenera kudzalipira K3 500 kuti amupangirenso chiphaso china. Koma malinga ndi Fulatira, mtengowu ukhala ukusinthasintha. +Maliro pa chisangalalo Mwambo wa chikondwerero choti dziko lino latha zaka 53 lili pa ufulu wodzilamurira lidasanduka chisoni pomwe ana 7 ndi bambo mmodzi adamwalira pokanganirana kulowa mbwalo la za masewero la Bingu National Stadium kumene kumayenera kuchitika mpira waulere. +Izi zidadziwika pomwe mtsogoleri wa dziko lino adatsogolera Amalawi pa mapemphero wolingalira za ufuluwo ku Bingu International Convention Centre (BICC) pomwe woyendetsa mwambowo mbusa Timothy Nyasulu adalengeza za omwalirawo. Iye adapempha anthu kuti akhale chete kwa mphindi imodzi polemekeza mizimu ya omwalirawo. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Wapolisi kuthandiza mmodzi mwa ana ku BNS Ndipo nduna ya zamalonda ndi mafakitale Joseph Mwanamvekha, yemwenso adali wapampando wa komiti yoyendetsa mwambowo, adatsimikiza za imfa ya anthuwo mapemphero ali mkati. Iye adati anthu oposa 40 adavulala pangoziyo. Nthambi yofalitsa nkhani za boma lidati anthu 65 adamwalira. +Mutharika ndi mayi Gertrude Mutharika adakazonda anthu amene adavulala pa chipwilikiticho ku Kamuzu Central Hospital. +Mutharika adati :Boma ndi lokonzeka kuthandiza pangoziyi. +Dziko la Malawi limakumbukira kuti latha zaka 53 kuchokera pamene mtsogoleri wa dziko lino Dr Hastings Kamuzu Banda adakwanitsa kupeza ufulu kuchokera kwa Angerezi amene adayamba kulamulira dziko lino mzaka za mma 1890. John Chilembwe, mmodzi mwa Amalawi oyambirira kufuna kumenyera ufuluwo adamwalira mu 1915. +Zikondwerero za chaka chino zinalipo kuyambira Lachitatu pa 5 July pomwe asilikali ndi achitetezo ena adayenda mmizinda ya Blantyre, Zomba ndi Mzuzu. +Ndipo chikondwerero chimayenera kufika pa mponda chimera pa masewero a Nyasa Big Bullets ndi Silver Strikers amene amayembekezeka kuchitika kumalo a ngoziyo. +Komatu galimoto za chipatala ndi zapolisi zidali kukangalika kuthandiza ovulala pa zisawawazo. +Koma polankhula ndi Tamvani zisangalalozo zisanachitike, Amalawi ena adati ngakhale dzikoli latha zaka 53 likudzilamulira maloto ena amene adalipo pomenyera ufulu wa dziko lino. +Yemwe adakhalapo sipikala wa Nyumba ya Malamulo, Sam Mpasu adati mMalawi wa zaka 53 ali panayi: Zina zasintha pangono, zina sizinasinthe, pomwe zina zaima kapena kubwerera mmbuyo. +Iye wati kunena mosapsatira zaka 53 sizidabweretse kusintha kwenikweni paulamuliro ndi kayendetsedwe ka maufulu a anthu mdziko muno. +Mwa zina, iye adati ulamuliro wa Kamuzu Banda udayesera kubwezeretsa ulimi mchimake pamene adakhazikitsa makampani otulutsa zinthu zina kunja zimene mu ulamuliro wa atsamunda zimakapangidwa kunja, koma zina sizikuyenda. +Adapereka zitsanzo za makampani a Sucoma, yomwe inkakonza shuga, Malawi Cotton yomwe inkaomba nsalu komanso British American Tobacco yomwe inkapanga ndudu ngati zina mwa zotsimikiza izi. Dziko lino lisanaladire ufulu, Mpasu adati zonsezi zinkabwera kuchokera kunja, ngakhale alimi ochuluka amene ankazilima mdziko muno ankatumiza kunja chifukwa adali Atsamunda. +Kamuzu adayesetsanso kulimbikitsa msika wa mbewu kudzera ku Admarc ndipo adaonetsetsa kuti manyamulidwe a mbewu ngosavuta chifukwa kudali sitima za panjanji zomwe zimanyamula katundu pa mtengo otsika kupita ku misika, watero Mpasu. +Ndipo mkulu wa bungwe loyanganira za momwe maphunziro akuyendera mdziko lino George Jobe wati pakutha pa zaka 53, Malawi amayenera kukhala ndi ntchito za umoyo za pamwamba motsatira chiyenerezo cha bungwe lalikulu loyanganira zaumoyo la World Health Organisation (WHO) koma mmalo mwake zinthu zambiri sizikuyenda. +Mpaka pano sitidayambe kukwaniritsa mlingo wa WHO oti K15 pa K100 iliyonse mbajeti izikhala ya za umoyo. Chiwerengero cha ogwira ntchito za chipatala chikadali chotsika kwambiri poyerekeza ndi anthu omwe dokotala mmodzi amawona pa tsiku, watero Jobe. +Ndipo kupatula zaumoyo, mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a zamaphunziro, Benedicto Kondowe wati sizoona kuti zaka 53 zingathe ana asukulu makamaka a kuma Yunivesite nkumakhala pakhomo miyezi yambiri chifukwa cha mavuto msukulu zawo. +Iye wati pa zaka zonsezi, atsogoleri amayenera kukhala atapanga njira zothandizira kuti kalendala ya sukulu kuyambira ku pulayimale mpaka ku Yunivesite isamasokonekere chifukwa kutereku nkulowetsa maphunziro pansi. +Posachedwapa, aphunzitsi adali pa sitalaka pa nkhani ya maphunziro ndipo tikunena pano ophunzira mma Yunivesite sadatsegulire chitsekereni miyezi ingapo yapitayo nkhani yake kayendetsedwe, adatero Kondowe. +Tinkakhala nyumba zoyandikana Mwayi wa banja umapezeka malo osiyanasiyana. Ena amapeza womanga naye banja mubasi, eetu paulendo, pomwe ena amakumana kutchalitchi. Koma kwa mphunzitsi wa sukulu ya utolankhani ya Malawi Institute of Journalism (MIJ) Jonathan Jere, sadathenso mtunda, koma adapeza mkhonde basi. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Pano Constance Kumwenda akutaya madzi pakhomo la Jere. Awiriwa adakwatirana chaka chathachi pa 5 December ku Mchengautuwa CCAP ndipo madyerero adachitikira ku hotelo ya Chenda, mumzinda wa Mzuzu. +Komatu si kuti Jere adayenda mofewa kuti apeze mkaziyu poti adali woyandikana nyumba, ayi ndithu. Mwana wammuna adakhetsera thukuta. +Jonathan ndi Constance patsiku lomwe adamanga woyera Ndimakhala moyandikana nyumba ndi makolo ake ku Chiwavi. Ndipo maso anga adayamba kudyerera pa iye patatha ingapo, adatero Jere. +Iye adati kwa miyezi 6 awiriwa sankacheza koma amangoonana ngati oyandikana nyumba. +Malinga ndi Jere, namwaliyu ndi namwino kuchipatala cha Mzuzu Central. +Pangonopangono adayamba kumufufuza ndipo atamva zoti palibenso tambala wina yemwe amazungulirazungulira kholali, adalimba mtima. +Apatu Jere adafufuza nambala yake ya foni kuchokera kwa anthu ena ndipo adaipeza. +Apa awiriwa adayamba kulumikizana ndipo posakhalitsa Jere adapempha kuti akakumane poduka mphepo ndi kukambitsana ziwiri, zitatu. +Komatu izi sizidatheke chifukwa namwaliyu adakanitsitsa kuti nthawi yokumana ndi Jere adalibe. +Ankati popeza tidali oyandikana nyumba anthu aziyesa zachibwana, adatero Jere. +Naye Jere sadagwe ulesi koma adayesayesabe mwayi wake, mpaka tsiku lina adangoti naye gululu! Sadachedwenso koma kumuuza zakukhosi kwake. +Pangonopangono ndidayamba kubooleza mpaka chibwenzi chidayamba ndithu, koma padatha mwezi ndikugubira ndithu, adatero Jere. +Iye adati polemekeza makolo komanso kuti kucheza kwawo kuziyenda bwino, adasamuka ndi kupeza nyumba ina kudera lina. +Adaonjezeranso kuti apa sadachitenso za bobobo, koma kuyamba kukonzekera za ukwati. +Koma popeza zokhoma sizilephera pa moyo, zinthu zidavuta kaamba ka mpingo. +Anthu ena sadafune kuti atuluke mpingo wake ndi kulowa wanga. Komabe pa uwiri wathu tidakambirana ndi kugwirizana kuti alowa mpingo wathu, adatero Jere. +Wotokosola mnzake diso akaseweza Khoti ya majisitireti ku Mangochi yalamula Joseph Mtambo wa zaka 25 kuti alipire K200 000 kapena akakhale kundende zaka zitatu chifukwa chovulaza mnzake. +Wachiwiri kwa mneneri wapolisi ya Mangochi Amina Daudi wati Mtambo adavulaza Jacob Nambo amene amamukaikira kuti amayenda ndi mkazi wake iye akapita ku Joni. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka An artists illustration of an arrested man Mtambo adapeza mauthenga achikondi mufoni ya mkazi wake. Iye adalemba uthenga kwa Nambo pafonipo kuti abwere kunyumba adzacheze pa 15 April. Atapita, Mtambo adamenya mnzakeyo ndi chitsulo ndi kumukolopola diso ndi waya, adatero Daudi. +Nambo adagonekedwa pachipatala cha Mangochi, asanamutumize kuchipatala chachikulu cha Zomba. Chipatalacho chidatsimikiza kuti Nambo adapweteka mmaso ndipo sakutha kuona. +Woimira boma pamlanduwo, Grace Mindozo adapempha bwalolo lipereke chilango chokhwima kwa Mtambo chifukwa chovulaza mnzake. Koma Mtambo adapempha bwalolo kuti limumvere chisoni chifukwa ndi mutu wa banja lake. +Ndipo woweruza Augustine Mizaya adati kupereka chilango chokhwima monga adapemphera apolisi kungakhale kulakwa chifukwa Nambo adachitanso kumutokosola mnzakeyo, mpaka kupita kunyumba kwake. +Mtambo ndi wa mmudzi mwa Mpinganjira, T/A Chimwala ku Mangochiko. +Otsutsa adzudzula MEC Bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) liyenera kutambasula bwino za pangano lake ndi bungwe limene likupereka zitupa za unzika la National Registration Bureau (NRB) pa zoti lidzagwiritsa ntchito zitupazo pa kalembera wa chisankho cha 2019, watero kadaulo pa ndale Mustafa Hussein. +Zipani za ndale, makamaka zotsutsa boma zakhala zikunena kuti chikonzero cha MEC nkufuna kudzathandiza chipani cha DPP kubera mavoti. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kalembera wa nzika ali mkati Mwati mudzagwiritsa ntchito zitupa za unzika kuti Amalawi alowe mkaundula wa zisankho. Apatu mpofunika kuti pamveke bwino chifukwa anthu akusokonekera, adatero Hussein. +Zipani zotsutsa boma zakhala zikudandaula ndi ganizo la MEC lodzagwiritsa ntchito zitupa za unzika kuti munthu adzalowe mkaundula wa chisankho cha 2019. +Zipanizi zakhala zikubweretsa nkhaniyi mNyumba ya Malamulo momwe aphungu akukambirana za bajeti ya 2017/18 ndipo moto weniweni udabuka lolemba lapitali pa nkhumano yomwe bungwe la MEC lidapangitsa kuti lifotokozerane ndi zipani nkhani yokhudza chisankhochi. +Nthumwi za zipani zotsutsazi makamaka za Malawi Congress Party ndi Peoples Party, zidabooleza kuti zikukhulupilira kuti ganizoli ndi njira imodzi yofuna kudzabera chisankhochi ndipo zidanenetsa kuti sizilola kuti pulaniyi idutse. +Phungu wa kummawa kwa boma la Dowa Richard Chimwendo-Banda wa Malawi Congress Party (MCP) adati akuona kuti MEC ikukonza zodzathandiza chipani cholamula cha Democratic Progressive (DPP) kubera chisankho. +Iye adati ndiwodabwa ndi kukakamira kwa bungwe la MEC kuti lidzagwiritse ntchito zitupa za unzika popanga kaundula wa anthu odzaponya voti chonsecho silikutengapo gawo lililonse pa zakapangidwe ka zitupazi. +Bungwe la MEC lidali kuti pomwe nthambi yopanga kalembera wa zitupazi imayamba ntchito yake? Tili ndi chikhulupiliro kuti ali ndi mapulani odzabera chisankho ndipo ndikuuzeni kuti ulendo uno sitikulekelerani, adatero Chimwendo-Banda. +Iye adati bungwe la MEC lisiye kulowerera ntchito za eni ndipo lipange pologalamu yake yakalembera wa mkaundula wa chisankho mmalo modalira kuwolokera pamsana pa anzawo. +Wampampando wa bungwe la MEC Jane Ansah yemwe ndi woweruza milandu ku khothi lalikulu la apilo sadakondwe ndi zomwe adanena aphunguwo ndipo adawadzudzula kuti nawo akulephera udindo wawo posafotokozera anthu awo za kufunika kwa zitupazi. +Iye adatsutsa zoti bungweli lili ndi maganizo odzabera chisankho mwanjira iliyonse koma kuti likufuna kuti anthu ovomerezeka okha ndiwo adzaponye voti mu 2019. +Nduna ya za mdziko ndi chitetezo Grace Chiumia adavomera kuti kalembera wa zitupa za unzika ikukumana ndi zokhoma monga kufaifa kwa zipangizo zogwiritsa ntchito. +Mafumu ayamikira kuyamba kwa ziphaso Mafumu mdziko muno ati kuyamba kwa ntchito yopanga ndi kupereka ziphaso zosonyeza unzika, ndi chiyambi chopititsa patsogolo ntchito za chitukuko zosiyanasiyana kaamba koti ndi njira imodzi yotsekera manga a katangale. +Dzana Lachinayi, mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adatsegulira ntchitoyi mumzinda wa Lilongwe ndipo pomva maganizo a mafumu, Tamvani idapeza kuti ntchitoyi ikomera mtundu wa Amalawi. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kachindamoto: Tikuyamika Mwa zina, mafumu adati zitupazi zithandiza kuti mchitidwe woba mankhwala mzipatala, kutulutsa ndi kulowetsa katundu mwachinyengo, kuthithikana mmisika ndi maukwati osalongosoka zichepe. +Timadandaula usana ndi usiku, chaka ndi chaka kuti mankhwala samalimba mchipatala cha Dedza. Si kuchipatala kokha, ayi, komanso ku Admarc kokagula chimanga ndi kuthithikana mmisika chifukwa chosazindikirana. +Ambiri mwa anthu omwe amapindula ndi ochoka kunja kaamba koti pozindikira kuti akuchita zachinyengo, amalawirira nkukakhala oyambirira kulandira thandizo. Amalawi akamabwera amapeza mankhwala atha, malo mumsika atha ngakhalenso chimanga chimene ku Admarc chatha, idatero mfumu yayikulu Kachindamoto ya mboma la Dedza Lachinayi. +Mfumu yaikulu Mlauli ya ku Neno, komwe ndi kufupi ndi malire a Malawi ndi Mozambique kudzera ku Mwanza, idati mafumu kumeneko adali pachipsinjo chachikulu pankhani yokhudza milandu ya malo kaamba kamaukwati osadziwika bwino. +Anthu amangochoka uko nkudzafunsira mkazi kuno ndiye poti padalibe zitupa, kumakhala kovuta kuwazindikira bola akangodziwako midzi ingapo nkumanamizira kuti amachokera kumeneko. Mapeto pake banja likavuta zimavuta kuweruza kwake ndipo akudza amapezeka kuti alanda malo, adatero Mlauli. +Inkosi Khosolo, ya mboma la Mzimba, idati chitupa nchitetezo choyamba kwa munthu kaamba poti kulikonse angapite, anthu amatha kumuzindikira. +Timachitira pangozi kapena munthu ukasowa kumene, ukakhala ndi chitupa, anthu amakuzindikira msanga nkukuthandiza, adatero Khosolo. +Moyo pachiswe: Ambiri akuzemba mankhwala otalikitsa moyo Amati phukusi la moyo umadzisungira wekha, koma kumene zikuloweraku, zikuonetsa kuti Amalawi ambiri omwe ali pamndandanda wolandira mankhwala otalikitsa moyo (ma ARV) akukwirira phukusi lawo pachulu cha aganga pozemba kulandira ndi kumwa mankhwalawa. +Malingana ndi zomwe Tamvani yapeza kuchokera kumgwirizano wa mabungwe olimbana ndi kufala kwa kachilombo ka HIV komwe kamayambitsa matenda a Edzi, anthu 20 mwa anthu 100 alionse oyenera kulandira mankhwalawa akuchita ukamberembere. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mankhwala otalikitsa moyo ngati awa safuna kudukiza munthu akayamba kumwa Wapampando wa mgwirizanowu, Maziko Matemba, wati ukamberemberewu ndi chiphe kaamba koti anthu otere sachedwa kugwidwa ndi chipwirikiti cha matenda chifukwa chitetezo cha mthupi mwawo chimatsika msanga. +Matemba adati kupatula kutsika kwa chitetezo cha mthupi, anthu omwe amati kuyamba kumwa mankhwalawa nkudukiza thupi lawo limapima kotero kuti silimvanso mankhwala alionse omwe angalandire akamva. +Tili ndi nkhawa yaikulu kwambiri chifukwa anthu otere ndiwo amabwezeretsa chitukuko cha dziko mmbuyo. Boma likuyesetsa kugula mankhwala kuti anthu ake azikhala nthawi yaitali ali ndi thanzi, koma iwo nkumathawanso, komwe kuli kusayamika, adatero Matemba. +Iye adati abambo ambiri komanso omwe amakhala mmatauni ndiwo akuchulukira kuzemba mankhwalawa kaamba ka manyazi, kuiwala kuti ali ndi udindo pamabanja awo ndi dziko lomwe. +Mafigala a bungwe la Malawi Network of Aids Organisations (Manaso) amasonyeza kuti mdziko muno muli anthu pafupifupi 850 000 omwe akuyenera kumalandira mankhwala otalikitsa moyo koma mwa anthuwa, mmadera akumidzi ndimo anthu ambiri amatsatira ndondomeko. +Mkulu wa Manaso, Abigail Dzimadzi, adati gulu lina lomwe likuchulutsa ukamberembere ndi achinyamata omwe safuna kuonekera kuti ali ndi kachilombo poopa kuti angadzasowe mabanja mtsogolo. +Chiopsezo chachikulu chili poti munthu yemwe sakulandira mankhwala ndiye ali nkuthekera kwakukulu kofalitsa kachilombo ndiye ngati achinyamata akuzemba, zikutanthauza kuti tikulimbana ndi nkhondo yomwe tikumenyananso tokhatokha, adatero Dzimadzi. +Nduna ya zaumoyo, Dr Peter Kumpalume, akuti nkhaniyi ndi yomvetsa chisoni kaamba kakuti boma limafunitsitsa vutoli litatheratu mdziko muno poti ena mwa anthu omwe dziko limataya chifukwa cha vutoli ndi ofunika mipando yautsogoleri. +Anthu ena auza Tamvani kuti nthawi zina anthu amazemba kukalandira mankhwala kaamba ka momwe amalandiridwira kuchipatala, koma unduna wa zaumoyo ndi bungwe la Manaso ati chifukwa ichi nchozizira polingalira za moyo wa munthu. +Mpofunika kuunika nkhani ya chinsinsi cha odwala chifukwa ena safuna kuonekera koma ali ndi mtima wofuna kumalandira thandizo. China ndi malankhulidwe a ogwira ntchito kuchipatala omwe amagwetsa anthu ulesi, adatero Lucy Banda, wapampando wa gulu lophunzitsa ndi kuyendera anthu omwe ali ndi kachilombo ka HIV ku Senga Bay, komwe akuti abambo ambiri amazemba kulandira mankhwalawa nkumatangwanika ndi usodzi. +Woyanganira nkhani za umoyo muunduna wa zaumoyo, Dr Charles Mwansambo, wati ichi nchimodzi mwa zifukwa zomwe boma, kudzera muundunawu, lidakhazikitsa pologalamu yoti kuchipatala kuzikhala malo apadera oti anthu azikalandirirako uphungu pankhani za Edzi ndi mankhwala otalikitsa moyo. +Panopa mzipatala zambiri muli malo apadera omwe anthu amakalandirirako uphungu, kuyezetsa magazi ndi kulandira mankhwala otalikitsa moyo. Ndiye nkhani ya chisinsiyo idakonzedwa, adatero Mwansambo. +Iye adatinso boma lidakhazikitsa pologalamu ya ma 90 atatu (90 90 90) kufuna kuti anthu athe kuzindikira kufunika kwa kutsatira ndondomeko ya mankhwala a ARV. +Ndondomekoyi imatanthauza kuti anthu 90 alionse pa anthu 100 akudziwa momwe alili mthupi mwawo; mwa anthu 90, 90 a iwo akulandira mankhwala otalikitsa moyo moyenerera; ndipo anthu ena 90 atetezedwa kukutenga kachilomboka. +Potsindika kufunika kolimbana ndi matendawa, naye sipikala wa Nyumba ya Malamulo, Richard Msowoya, adapempha aphungu a nyumbayi kuti kupatula kudalira bajeti ya boma, azikhala ndi mapologalamu opezera zipangizo zomenyera nkhondoyi. +Pempholi adaliperekanso kwa akuluakulu a mabungwe pamisonkhano yomwe nyumbayi idachititsa mwezi wa August wa aphungu ndi amabungwe pankhani yolimbana ndi matendawa mchigawo cha maiko a kummwera kwa Africa, yomwe imadziwika kuti Sadc-PF. +TB ya kumsana imapha ziwalo Dokotala wothandiza anthu omwe ali ndi vuto la kufa kwa ziwalo kuchipatala cha Kachere Rehabilitation Centre mumzinda wa Blantyre, Veronica Mughogho, wati TB ya kumsana imapha ziwalo. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Iye adati padakalipano, ambiri mwa anthu omwe akumabwera kudzalandira thandizo kubungweli, gwero lake likumakhala TB ya kumsana yomwe imatchedwa spinal TB mChingerezi. +Zikuoneka kuti ambiri sakuyidziwa nchifukwa chake anthu amapita kuchipatala mochedwa zinthu zitafika kale poipa, adatero iye. +Masewero ngati awa amathandiza ziwalo ziyambenso kugwira ntchito Mughogho adati nthendayi imayamba pangonopangono ndi kupweteka kwa msana ndipo munthu amanyengeka ndi kumangomwa mankhwala opha ululu. +Kupweteka kwa msanaku kumapitirira kwa nthawi yaitali ndipo ululu wake umachulukira. Munthu akaona kuti wakhala nthawi yotalikirapo akumva ululuwu, akuyenera kukayezetsa mwamsanga kuti alandire thandizo mwamsanga zinthu zisanafike poipa monga kufa ziwalo, adatero dokotalayu. +Iye adati zizindikiro zina ndi monga kumva kuzizira, kutuluka thukuta usiku, kuonda komanso kutuluka chotupa pantchafu. Adaonjeza kuti tizilombo tomwe timayambitsa nthendayi ndi tofanana ndi tomwe timayambitsa TB ya mmapapo yomwe imadziwika kuti chifuwa chachikulu. +Kusiyana kwake nkwakuti tizilomboti timakhamukira kumsana ndi kumadya nyama ndi fupa la kumsanandipo mafinya amayamba kutuluka ndipo amalowa mkati mwa msana ndi kufinya mtsempha waukulu umene umalumikiza uthenga kuchokera kubongo kupita ku ziwalo zina za thupi, adatero Mughogho. +Iye adaonjeza kuti izi zikapitirira, mtsemphawo umatha kuduka ndipo zosatira zake zimakhala kufa kwa mbali ya thupi kuchokera pomwe padukapo, kupita kumunsi. +Mughogho adati ngati TB yazindikiridwa munthu atafa kale ziwalo, munthuyo amalandira thandizo la mankhwala kenako amatumizidwa ku malo ochitirako masewero. +Ziwalo zimatha kuyambiranso kugwira ntchito ngati mtsemphawo siunaonongeke kwambiri koma ukaonongekeratu, munthu amalumala mpaka kalekale. Ndi chifukwa chake tikuti anthu akuyenera kukayezetsa akayamba kuona zizindikirozi kuti alandire thandizo la mankhwala mwa msanga, adatero dokotalayu. +Kusamala nazale ya fodya Pamene alimi ali pakalikiliki kusosa, alimi, makamaka a fodya ali mmalingaliro okonza nazale. +STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi mtsogoleri wa alimi a fodya omwe ndi mamembala a bungwe la Tobacco Association of Malawi (Tama) ku Bolero mboma la Rumphi Isaac Msiska za kusamalira nazale. Adacheza motere: Escom in free-for-all fuel scam Wait gets longer Secrecy over party funders Tandifotokozerani kuti pokonza nazale ya fodya mlimi amayenera kuyangana zinthu ziti? Choyamba, popanga nazale ya fodya nkupeza malo omwe ali pafupi ndi madzi chifukwa nazale ya fodya imafuna kuthirira kawiri tsiku lililonse osaphonyetsa. Pamafunika kuthirira mmawa kenako madzulo ndiye ngati yatalikirana ndi madzi, pali vuto lalikulu zedi pamenepo. +Alimi amayenera kuyanganira bwino fodya pa nazale Malo apezeka, chotsatira nchiyani? Malo akapezeka pamafunika kuonetsetsa kuti mpofewa. Ngati pali polimba, ntchito ya madzi ija imayambira pamenepo kuwazapo kuti pafewe kenako nkugaulapo bwinobwino. Tikatha kugaula, timayikapo zinyalala nkutentha kaamba kuti ngati mnthaka mumakhala njere za mbewu zina zomwe sizifunika kumerera limodzi ndi fodya zife. +Zonsezi zatheka chimatsatira nchiyani? Iyi ndinthawi yoyamba kupanga mabedi ndipo popanga mabediwo palinso zina zomwe timayenera kutsatira. Timatenga madzi nkuthiramo mankhwala omwe amathandiza kupha kapena kuthamangitsa Nyerere zomwe tikazilekerera zimakoka njere tikabzala. Tikawazapo, timapanga mabedi a nazale ya fodya kuyembekezera kuti nthawi ina iliyonse tifesa fodya panazale. +Tsiku lofesa kumakhala zotani? Tsiku lofesa pamafunika kuti zinthu zonse zofunikira ngati zija ndalongosolazi zikhale pafupi koma china chomwe sindidanenepo ndi udzu waa kansichi otchingira pamwamba pa mbewu zathu. Udzuwu ndi wachilengedwe koma umayenera kukhala pafupi oduladula kale kuti tikangofesa, nthawi yomweyo titchinge pamwamba. +Mumafesa bwanji? Choyamba kansichi wathu ali apo, timatenga kheni yothiririra nkuyikamo madzi ndi mbewu ya fodya nkumachita ngati tikuthirira ndiye mbewu zimatulukira limodzi ndi madzi aja. Tikatha timatchingira bwinobwino ndi kansichi uja. Tikatero, ntchito yothirira yayambika ndipo timati uku tikuthirira nazale, kwinaku tikukonza kumunda kupangiratu mizere kuti tizichepetsako ntchito ina pangonopangono. +Nazale yabwino imafunika kukhala ndi mabedi angati? Nazale ikhoza kukhala ndi mabedi angapo koma pamakhala bedi limodzi lomwe limakhala kholo. Zonse timafesa pabedi la kholo lija pofuna kuchepetsa ntchito malinga ndi zomwe ndanena kuti pamakhala kuthirira mwakathithi. Mbande zikakula pangono, timazisamutsira pa mabedi ena aja kuti zizipuma bwino koma kuthirira mwakathithi kumapitirirabe. +Nzololedwa kubwereza malo a nazale potengera kuti malo opezeka madzi ndi wovuta? Nzosaloledwa kubwereza malo a nazale. Mbewu zina zimakhala ndi matenda akeake ndiye mukachotsapo, matenda kapena tizilombo timatsalira pamalopo choncho podzabzala mbewu Inayo imakumana ndi vutoli ikadali yaingono kwambiri nkuvutika kakulidwe. +Ndalama za mthandizi siziphula kanthu Pomwe anthu akumudzi amayembekezera kuti kuonjezera kwa ndalama zomwe azipeza akagwira ntchito ya mthandizi kuchepetsa ululu wa njala, Tamvani wapeza kuti vutoli langosintha mmafigala koma moyo ukadali chimodzimodzi. +Boma litalengeza mu August kuti laonjezera ndalama za pologalamuyi, padali chiyembekezo chakuti banja lizitha kugula matumba awiri a chimanga a 50kg likagwira ntchito ya chitukuko kapena thumba limodzi kuchokera ku ndalama ya mtukula pakhomo. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Anthu akumudzi amapulumukira ntchito za Mthandizi ngati izi Nduna ya zachuma Goodall Gondwe idalengeza kuti ndalama za pologalamuyi zawonjezeredwa kufika pa K13.2 biliyoni kuti banja likagwira ntchito ya chitukuko lizilandira K14 400 ndipo mabanja olandira ndalama za mtukula pakhomo azilandira K6 500 pamwezi. +Gondwe adati boma lidapanga izi pofuna kuti anthu ambiri, makamaka akumudzi, athe kupeza ndalama zogulira chimanga kumisika ya Admarc pofuna kupulumutsa anthu pafupifupi 6.5 miliyoni omwe akukhudzidwa ndi njala chaka chino. +Nkhaniyi idatanthauza kuti ndi K14 400, banja likadamagula matumba awiri a chimanga pamtengo wakale wa K5 500 ndi kutsala ndi K3 400 yopangira zinthu zina, pomwe a mtukula pakhomo bwenzi akugula thumba limodzi nkutsala ndi K1 000 yapamwamba. +Lipoti loona za chiwerengero cha anthu mMalawi muno la National Statistical Office (NSO) la mchaka cha 2000, limasonyeza kuti banja lililonse lili ndi anthu pafupifupi 5 ndipo malingana ndi buku la ndondomeko zapamwamba za ulimi, munthu mmodzi wamkulu amafunika kudya matumba 6 olemera 50kg pachaka. +Izi zikutanthauza kuti pamwezi munthu mmodzi amafunika makilogalamu 25, kuyimirira matumba awiri ndi kota pa banja la anthu 5 pamwezi umodzi. +Kutengera pamtengo watsopano wa chimanga wa K12 500, banja lodalira ntchito ya chitukuko lizikwanitsa kugula thumba limodzi la chimanga nkutsala ndi K1 800 pomwe odalira mtukula pakhomo aziyenera kuonjezera K6 000 kuti agule thumba limodzi. +Mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, adalengeza atangofika kumene kuchokera ku America kuti Admarc ikweze mtengo wa chimanga kufika pa K12 500. +Ndalamula bungwe la Admarc kuti ligulitse chimanga pamtengo wa K250 pakilogalamu. Uwu ndi mtengo womwe Admarc imagulira chimanga kuchokera kwa alimi, adatero Mutharika. +Mneneri wa bungwe la Admarc Agnes Chikoko adati padalibe njira ina yopewera kukwenzaku kaamba kakuti mtengowu ndi womwe bungweli limagulira kwa alimi, kutanthauza kuti likungofuna kubweza zake kuti chaka cha mawa lidzathenso kugula. +Umenewu ndiye mtengo womwe timagulira kuchokera kwa alimi ndiye sitingagulitse pamtengo wotsikira pamenepa chifukwa tidagula ndi ndalama za ngongole zofunika kubweza kuti chaka chamawa tidzathe kupeza ngongole ina, adatero Chikoko. +Iye adati pakalipano bungweli lili ndi chimanga chokwanira kudzafika nyengo yokolola pomwe anthu angadzayambe kudalira zakumunda moti kulephera kupeza chakudya, akhala mavuto ena kwa anthu. +Bungwe la Alliance Capital Limited ndi bungwe la Transformation Alliance adauza nyuzipepala ya Fuko yomwe imasindikizidwa ndi kampani ya Nation Publications Limited (NPL) kuti mtengo watsopanowu upangitsa kuti mavenda nawo akweze mitengo yawo mosaganizira. +Potsatira chenjezoli, Tamvani adafufuza mitengo mmisika ina ndipo adapeza kuti kwa Goliati ku Thyolo, chimanga chili pa K12 500 pa thumba la 50kg; Kasungu K9 000, kwa Che Musa ku Blantyre ndi K13 000, Zingwangwa K14 000 ndipo Mzuzu K11 250 pa thumba la 50kg. +Anthu omwe adalankhula ndi Tamvani adati boma likhoza kupereka zifukwa zokwezera mtengo wa chimangawu koma zifukwazi sizikutanthauza kuti anthu apepukidwa chifukwa agulabe chimangacho kuti apulumuke. +Boma likhoza kupereka zifukwa zambirimbiri zokwezera mtengowu koma zifukwazo sizikutanthauza kuti anthu apeza chimanga mosavuta komanso afune asafune, akakamizidwa kugula kuti asafe ndi njala, adatero Damiano Limbani wa ku Katondo mboma la Lilongwe. +Aureliano Banda wa ku Nambuma mboma lomweli adati iye ndiwokayika ngati kukweza mtengoku kudadutsa mukufuNsa maganizo a anthu ndi kuunika momwe anthu aliLi pa nkhani ya zachuma. +Akadakhala kuti akuluakuluwa amapita mmidzi mwenimweni kukaona momwe zinthu zilili, si bwenzi kusintha kwinaku kukukhala momwe kumakhaliramu, ayi. Mwachitsanzo, mmidzimu muli umphawi wadzaoneni wosowa kolowera nawo, adatero Banda. +Janet Zgambo, wabizinesi mumsika wa Mchesi, adati zoona zake za kukula kwa vutoli zioneka ndi momwe anthu azipezekera mmisika ya Admarc, makamaka mmiyezi yomwe ikudzayi. +Tikuchita bwanji ndi matewera? Thewera loti lagwiritsidwa ntchito limaipa mmaso komanso kudetsa kukhosi. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mwina likakhala la mwana wako, komabe ambiri limativuta kuyangana, kuligwira kapena kuchapa kumene. +Utchisi wathewera la nsalu umaonekera komanso kusautsa anthu pakhomo. +Amayi ena opanda dongosolo amatha kusunga matewera ogwiritsa ntchito kwa nthawi yaitali zomwe zimasokoneza pakhomo. +Mmaganizo awo amayi oterewa amati chimbudzi cha mwana nchosachititsa nyansi chasiyana ndi munthu wamkulu. +Koma izi sizoona. Chimbudzi ndi chimbudzi basi. Sichikondweretsa kuchiona. +Kuphatikiza apo, kulephera kusamala chimbudzi choti mwina muli matenda kungapangitse kuti matendawo afale mosavuta. +Tsopano kubwera kwa matewera a pulasitiki, aja timangotaya tikagwiritsa ntchito, kwadzanso ndi utchisi wake omwe umakhudza anthu ochuluka mmadera omwe tikukhala. +Basitu, amayi ena omwe amagwiritsa ntchito matewerawa amangotayapo mwachisawawa nkumapatsa agalu zochita. +Mukudziwa inu khalidwe la galu. Kungotayapo matewerawa poyerayera kumapangitsa agalu kuti akoke izi nkumakasiya mmakomo mwa anthu ena kapena mmisewu kumene. +Koma aliponso amayi ena omwe sadikira galu kuti achiteizi. Ngati alibe dzala kapena malo ena osunga zinyalala, amangoponyapo matewerawa pali ponse bola zachoka pakhomo lawo. +Kukhala kotereku nkosokoneza. Thewera la mwana wako lisapsinje anthu okuzungulira. +Pamene tikukhala mmaderamu timayenera kuonetsetsa kuti zochita zanthu zisasokoneze moyo wa anzathu. +Iwe usamapeze mtendere pochita chinthu chomwe chichotse mtendere wa wina. +Tisanagwiritse ntchito thewera la pulasitiki tiganizire kuti tilisamala bwanji kuti lithere pakhomo pathupo, lisakafike pakhomo pa mnzathu kapenanso kuonedwa ndi ena omwe sizikuwakhudza. +Mmadera tikukhalamu tatopa ndi mchitidwe womangotaya matewera paliponse. +Tidziwane ndi Enock Balakasi wa Joy Radio Atolankhani mdziko muno amakumana ndi zokhoma zambiri makamaka pofuna zoti auze mtundu wa Amalawi. Mwa zifukwa zina, kusoweka kwa lamulo lothandiza kuti atolankhaniwa azitha kutola nkhani paliponse popanda chowapinga ndi nkhani yomwe pakalipano ili mkamwamkamwa. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Enock Balakasi wa kanema ndi wayilesi ya Joy pankhaniyi. +Balakasi: Ufulu wolemba uli papepala basi Dzina lako ndani mbale? Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Dzina langa ndi Enock Balakasi, wachiwiri mbanja la ana 7. Ndimachokera mmudzi mwa Matandika kwa T/A Nkula mboma la Machinga. Pano ndimayanganira ofesi ya Lilongwe ya kanema ndi wayilesi ya Joy koma ndidalembedwa ntchito ngati mkonzi ndi mtolankhani. +Udayamba liti za utolankhani? Utolankhani ndidauyamba mu 2007 nditamaliza maphunziro anga kusukulu yophunzitsa ntchito ya Blantyre Business College. Yemwe adandilimbikitsa kuti nditsatire za utolankhani ndi malume anga a Dr Rodrick Mulonya ndipo pano ndikupitirizabe maphunziro a zautolankhani chifukwa sindidafike pomwe ndimafuna. +Zimaonekatu ngati atolankhani mdziko muno amavutika kuti apeze nkhani, kodi vuto nchiyani? Choyamba ndivomereze kuti ufulu wolankhula ndi kulemba ulipo koma kandodo kokwapulira kamakhala mkhundu. Ufuluwu umaoneka kuti uli papepala basi koma kuti ukwaniritsidwe pamavuta. Mwachitsanzo chabe, atolankhani akhala akugubuduka kupempha kuti pakhale lamulo lowapatsa mphamvu zogogoda khomo lililonse kukatola nkhani, lija amati Access to Information (ATI) koma zikuoneka kuti akuluakulu ena ali ndi maganizo ena pankhani imeneyi. Lamuloli litangotheka, zonse zikhoza kusintha nkumayenda bwino pantchito ya utolankhani. +Nkani ina ndiyakuti nthawi zambiri mdziko muno pamatenga nthawi kuti chomwe chachitika chimveke monga momwe maiko a anzathu amachitira, pamenepanso ndi nkhani ya lamulo lomweli? Mbali ina tikhoza kunena kuti lamuloli limatengapo gawo lake koma kwakukulu ndi kusowa kwa zipangizo. Nyumba zambiri zoulutsa ndi kusindikiza nkhani muno mu Malawi zilibe zipangizo zokwanira ngati momwe makampani akunja mukunenawo. Mwachitsanzo, kuno kwathu pakakhala zochitika, nthawi zambiri timadalira omwe akonza zochitikazo kuti anyamule atolankhani komwe kuli kulakwitsa chifukwa pamenepo mumakhala kuti mwayamba kale kugwa mbali ya okutenganiwo. Njira yabwino ikadakhala yoti makampani oulutsa ndi kusindikiza nkhani akhale ndi zipangizo zawozawo kuti akafuna kukatola nkhani asamakhale ndi mbali ina iliyonse. +Watsalawatsala Lachiwiri likudzali, Chisankho chachibwereza chayandikira Mitima ili dyokodyoko kufuna kudziwa kuti kodi ndani adzasenze udindo wotumikira anthu mmadera osiyanasiyana pachisankho chachibwereza chomwe chiliko Lachiwiri likudzali malingana ndi ndondomeko ya bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC). +Malingana ndi bungweli, pakutha kwa sabata yamawa, anthu akhala akudziwa yemwe adzakhale phungu wa kunyumba ya malamulo kudera la kumadzulo kwa boma la Mchinji komanso makhansala mmawodi a Bunda mboma la Kasungu, Kaliyeka mboma la Lilongwe, Bembeke mboma la Dedza ndi Sadzi mboma la Zomba. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mphamvu yosankha atsogoleri yagona mwa anthu ngati awa Zisankho zachibwereza zimachitika ngati yemwe adali woimira dera wamwalira kapena pazifukwa zina watula pansi udindo ndipo munthu wina akuyenera kulowa mmalo mwake kuti apitirize ntchito yake. +Dyokodyokoyu waonekera pomwe Tamvani adazungulira mzipani zonse zomwe zikupikisana nawo pazichisankhozi kumva maganizo awo ndipo zosangalatsa nzakuti chipani chilichonse chalumbira kudzatenga mipando yonse. +Woyendetsa zisankho mchipani cholamula cha Democratic Progressive Party (DPP) Kondwani Nankhumwa adati palibe chokaikitsa kuti oyimirira chipanichi adzapambana chifukwa zonse zikuoneka kumisonkhano ya kampeni. +Kulikonse komwe tayenda kukachita msonkhano wakampeni talandira sapoti yaikulu kwambiri moti ena aiwale chifukwa oyimirira chipani cha DPP akudzatenga mipando yonse mosakaikitsa, adatero Nankhumwa. +Naye woyendetsa zisankho mchipani cha Malawi Congress Party (MCP) Maxwell Thyolera adati onse otsatira chipanichi akonzekere chisangalalo pakutha kwa tsiku Lachiwiri pa 1 November chifukwa oyimirira chipanichi akudzaonetsa mphamvu za chipani. +Chipani cha MCP ndi chipani chachikulu kwambiri ndipo aliyense amadziwa zimenezi. Pano ndikuuzeni kuti dzuwa likamadzati thii kulowa Lachiwiri, kudzakhala chisangalalo chokhachokha kuchipani cha Congress, adatero Thyolera. +Kumbali yake, wogwirizira mpando wa mtsogoleri wa chipani cha Peoples (PP) Uladi Mussa adati chilichonse chakonzedwa kale chomwe chatsala nkuti oyimirira chipanichi mmipando yanenedwayi adzalandire nyota zawo. +Iye adati chokhumudwitsa nchimodzi chokha chomwe ndi nthawi yopangira kampeni yomwe yaperekedwa ndi bungwe loyendetsa zisankho, koma ngakhale zili chomwechi, chipanichi chidzapambana mosavuta. +Sitikuyangana mmbuyo koma mtsogolo basi. Ngakhale apereka nthawi yochepa ya kampeni [masiku 9 okha], ife tilibe nkhawa. Anthu amachidziwa kale ndi kuchikonda chipani cha PP kotero akungoyembekeza kudzatsimikizira izi pa 1 November, adatero Mussa. +Mneneri wa chipani cha United Democratic Front (UDF) Ken Ndanga adati chipanichi chakhala chikukumana ndi akuluakulu a mmadera momwe muchitike chisankhochi kukambirana za momwe angayendetsere nkhani ya chisankhoyi. +Atsogoleri onse a mmadera momwe mudzakhale zisankho atitsimikizira kuti muli odzayimirira chipani cha UDF amphamvu ndipo tikupanga kampeni yamphamvu yomwe tikukhulupirira kuti palibenso wina yemwe angapambane kuposa oyimirira UDF, adatero Ndanga. +Iye adati pomwe padali vuto ndi dera lomwe kukupikisana ofuna mpando wa uphungu wa kumadzulo kwa boma la Mchinji komwe ntchito yofufuza odzayimirira chipanichi idali mkati pofika Lachiwiri lathali pomwe amalankhula ndi Tamvani. +Sabata ziwiri zapitazi, zipani za ndale zakhala zili kalikiriki kuyenda mmadera onse momwe muchitike zisankhozi kukopa anthu kuti adzaponyere voti oyimirira zipani zawo ndipo chosangalatsa nchakuti pamisonkhano yonseyi sipadamvekeko zazipolowe. +Wachiwiri kwa mneneri wa bungwe la MEC Richard Mveriwa adati chosangalatsa nchakuti chitsegulireni misonkhano yokopa anthuyi pa 20 October, zinthu zakhala zikuyenda bwino popanda zokokanakokana pakati pa zipani kapena zimpani ndi bungweli. +Iye adati anthu odzathandizira kuyendetsa chisankhochi adayamba maphunziro awo pa 27 October ndipo misonkhano ya kampeni idzatsekedwa mawa pa 30 October, kukonzekera kudzaponya voti pa 1 November. +Kumbali yathu, chilichonse chili mmalo mwake moti ndife okonzeka kudzayendetsa chisankho chimenechi mosavuta. Chomwe tingapemphe Amalawi nchakuti apitirize kusunga mwambo kuyambira pano mpaka chisankho chidzathe, adatero Mveriwa. +Malingana ndi ndondomeko ya kayendetsedwe ka chisankhochi, zipangizo zoponyera voti zidzayamba kuperekedwa mmalo a mavoti pa 30 October tsiku lotseka kampeni. Pa 1 November 2016, ndi tsiku loponyera voti ndipo pa 2 mpaka pa 4 November adzakhala masiku owerenga mavoti ndi kuulutsa opambana pomwe pa 7 November mpomwe maina a opambana adzasindikizidwe. +Kufumuka si kulakwa, olemekezeka! Nkhani ili mkamwamkamwa panopa ndi yoti nduna ya zaulimi, mthirira ndi chitukuko cha madzi, George Chaponda, kudzanso mkulu wa bungwe la Admarc, Foster Mulumbe, atule pansi maudindo awo kuti komiti yomwe Pulezidenti Peter Mutharika wakhazikitsa kuti ifufuze za nkhani ya chimanga chomwe boma lidagula kudziko la Zambia igwire bwino ntchito yake. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Chaponda wanenetsa kuti satula pansi udindo wake monga nduna. Nayenso Mulumbe wati sanenapo kanthu pankhaniyi. Chaponda wati sakuonapo chomwe adalakwa ngakhale kuti akukhudzidwa ndi nkhani yogula chimanga kuchokera kudziko la Zambia kuti chipulumutse anthu kunjala yomwe yagwa mdziko muno. +Zomwe zikumveka nzakuti pakukhala ngati padalowa chinyengo malinga ndi mmene malonda a chimangawo adayendera. Izi zili choncho chifukwa mmalo mongogula chimangacho motchipa ku Zambia Cooperative Federation (ZCF) ogulitsa chimanga ku Zambia, boma la Malawi, kudzera ku bungwe la Admarc, lidaganiza zogula chimangacho pamtengo wodula pogwiritsa ntchito kampani yomwe si ya boma la Zambia yotchedwa Kaloswe Commuter and Courier Limited ngati mkhalapakati. +Chifukwa chogwiritsa ntchito kampaniyo pogula chimanga chokwana matani 100 000, boma la Malawi lidasakaza ndalama zokwana K26 biliyoni zomwe lidakongola kubanki ya Eastern and Southern African and Development, lomwe limadziwikanso ngati PTA Bank. +Achikhala kuti adangogula chimangacho ku ZCF, boma likadagwiritsa ndalama zokwana pafupifupi K15 biliyoni basi. Izi zikutanthauza kuti boma la Malawi lidasakaza ndalama zokwana pafupifupi K9.5 biliyoni zapamwamba pogula chimangacho kudzera kukampani ya Kaloswe Commuter and Courier Limited. Ho, zichulukirenji ndalama! Funso nkumati: Padali chifukwa chanji chosankhira njira yogula chimanga pamtengo wokwera chomwechi pomwe njira idalipo yopezera chimangacho pamtengo wotsika? Apa mpamene pakhota nyani mchira, nchifukwa chake Amalawi ambiri, kuphatikizapo a mabungwe osiyanasiyana akuganiza kuti pena pake payenera kuti padalowa chinyengowina ayenera kuti adanyambitapo kena kake! Ndikukumbukira nthawi ina yake Joe Manduwa, yemwe adali wachiwiri kwa nduna ya zaulimi nthawi ya Bakili Muluzi, ankayankha mlandundaiwala pangono kuti udali mlandu wanji poti ndi kale limene lija. Manduwa, mwa iye yekha, adatula pansi mpando wake wonona ponena kuti ankafuna kuti chilungamo chioneke bwinobwino pamlandu wake posatengera kuti wavala ministerial jacket (jekete ya uminisitala). +Mwina a Chaponda ndi a Mulumbe, akadatengerapo phunziro pa zomwe adachita Manduwa potula pansi udindo kuti zofufuza ziyende myaa popanda zokayikitsa kapena zopingapinga. Ngati ofufuzawo sawapeza kulakwa pa zomwe zidachitikazo, sindikukayika kuti Pulezidenti Mutharika adzawabwezera pantchito zawo zofufuzazo zikadzatha. +Ndime ya vakabu yapita, koma samalani Ena mwa anthu okhala mumzinda wa Mzuzu ati ngakhale bwalo lounika za malamulo oyendetsera dziko lino lidati lamulo la vakabu nlosayenera, apolisi ayenera kukhala tcheru pogwiritsa ntchito malamulo ena owapatsa mphamvu zomanga anthu opanda chilolezo cha bwalo la milandu(warrant of arrest)kuopa zigawenga kutengerapo mpata wozunguza anthu usiku. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Lachiwiri lapitali oweruza milandu atatu: Zione Ntaba, Micheal Mtambo ndi Sylvester Kalembera adalamula kuti gawo 184(1) (c) ya malamulo a dziko lino ngolakwika ndipo sakugwirizana ndi ulamuliro wa demokalase omwe uli mdziko lino. +Venda wina wogulitsa majumbo Mayeso Gwanda ndiye adatengera nkhaniyi ku bwaloli mothandizidwa ndi woimira milandu Mandala Mambulasa. +Kadadzera: Anthu asadere nkhawa Pomwe Msangulutso udacheza ndi ena mwa anthu okhala mzinda wa Mzuzu, mmodzi mwa anthuwa Chrissy Phiri yemwe amakhala ku Masasa mzindawu adati sadasangalale ndi kuchotsa kwa lamuloli ata kaamba koti zigawenga zipezerapo danga lozunguza anthu maka usiku. +Phiri adati zigandanga zambiri zimaenda usiku ndipo ndi lamulo la vakabu, apolisi amatha kuzilonda mpaka kuzigwira. +Ndili ndi mantha kuti zigawenga zikhonza kupezerapo mwai pakuchotsa kwa ndimeyi, adatero Phiri. +Pomwe Frank Chisale adati vakabu imalakwika poti pena apolisi amanyamula aliyense ndi wosalakwa omwe. +Nthawi zina amanyamula ndi opita kumapemphero ausiku omwe, adatero Chisale. +Iye adati apolisi amayenera kunyamula okhawo omwe akuganiziridwa kuti ndi zigawenga kapena apalamula mlandu. +Koma polankhulapo, mneneri wa ku likulu la polisi ku Lilongwe James Kadadzera adati anthu asadere nkhawa kaamba koti apolisi azikwidzingabe oganiziridwa kuti ndi zigawenga pogwiritsa ntchito malamulo ena. +Kadadzera adati izi zithandiza kuchepetsa umbava ndi Umbanda ngakhale achotsa ndime ina ya ya gawo 184(1) ya malamulo yomwe imakamba za vakabu. Iye adati lamuloli lithandiza kutsatira ndi kutsekera mchitokosi oganiziridwawa ngakhale oyenda pansi koma alibe zida sazinjatidwa. +Okha okhawo omwe apezeka ndi zida zowopsa ndiwo azikwidzingidwa ndi unyolo mpaka kuimbidwa mlandu poyesetsa kuteteza mzika za dziko lino, adatero Kadadzera. +Ndime yachotsedwayi imapatsa mphamvu apolisi kugwira ndi kutsekera mchitokosi munthu aliyense wooneka kuti akhoza kudzetsa chisokonezo kapena ali ndi zolinga zochita zosemphana ndi malamulo kumene kaya ndi mu msewu kapena mmalo ena ndi ena. +Bwaloli lidanenetsa kuti ndi kandime kokhaka komwe kali kosayenera ndipo ndime zina zonse mgawo lonselo zikhoza kugwiritsidwa ntchito. +Kumawachenjeza anawa Ndimakumbuka kuti masiku adzanawo, nkhani zogwiririra anazi zisanafale kwenikweni, mayi wanga ankatikhazika pansi, ine ndi achemwali anga, kutiuza kuti kunjaku kuli anthu ena aupandu omwe amakhoza kuseweretsa matupi a ana nkuwachita chipongwe. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Apatu nkuti tili achichepere; zaka zathu zili pakati pa zisanu ndi khumi. +Adachenjeza mayi kuti pali ziwalo zina pathupi zomwe munthu wina tisamamulole kuzigwira ndipo adanenetsa kuti wina atakugwira modabwitsa-kaya ndi malume, mlongo wako kapena mphuzitsi-ukuwe, uthawe nkuwadziwitsa mayi kapena munthu wina wachikulire. +Adachenjezaso kuti aphuzitsi amphongo osazolowerana nawo kusukulu. Adanenetsa kuti aphuzitsi aamuna usakakhale nawo wekha muofesi, kaya mkalasi ndipo adati akakutuma kuti ukasiye makope kunyumba kapena kuti ukawasesere kunyumbako, uwakanire ndipo akakati wachita mwano adzathana ndi mayiwo. +Adakambaponso za aphuzitsi opereka malikisi ochuluka pomwe mwana walakwa. Adati oterewa tikachenjere nawo chifukwa izi sachita zaulere; amafuna malipiro tsiku lina. +Zomangolandira timphatso ngati switi, bisiketi kaya ndalama kwa anthu osawadziwa bwino adakaniza mayi. Pakhomo ngati pali mnyamata kapena bambo wogwira ntchito, padalinso malire pakachezedwe naye popewa kuti angatikole msampha. +Padali zambiri zomwe mayi ankatilankhula, mwina ankaonjeza kumene, koma adatitsegula maso za kuopsa kwa anthu mdziko limene timakulamo. +Malangizowa adakhazika mmitu mwathu kotero kuti sikudali kwapafupi kuti wina atitchere ndale chifukwa mayi adali ataunikira za nzeru zosiyanasiyana zomwe anthu amagwiritsa nthito pofuna kuchita nkhanza kwa ana. +Choncho nthawi zonse ndikamva kapena kuwerenga za mwana amene wagwiriridwa sindilephera kulingalira ngati makolo a mwanayo adayesapo kumuchenjeza za mchitidwewu womwe ukukhala ngati wafalikira mdziko lathu. +Malangizowa sangagwire ntchito nthawi zonse chifukwa nthawi zina anawa amangokakamizidwa mwadzidzidzi ndi munthu wamphamvu zoti sangalimbane naye. +Komatu kawirikawiri tikumva kuti anthu omwe akugwiririra anawa amawanyengerera ndi switi, ndalama ndi zina zoterozo. Kusonyeza kuti amabwera momuwenderera mwanayu pokambirana naye momupusitsa. +Osiyidwa pachilumba cha Ruo alira koto! Ndi 5 koloko mmawa, Belita Zakeyu wa mmudzi mwa Manthenga kwa T/A Mlolo mboma la Nsanje wafika kale mmanda a Chikoje kudzatola nkhuni. Iye akufuna akagulitse nkhunizo tsidya linalo, komwe ndi mdziko la Mozambique komwenso akufuna akaguleko chimanga. +Manda a Chikoje ndi dzina chabe tsopano poti madzi osefukira adakokolola mabokosi a maliro nkuwataya kutali. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ruo watsopano yemwe wabweretsa mavuto kwa Mlolo Zakeyu, yemwe sakudziwa zaka zake, akusunga ana 9. Anayi ndi ake pamene enawo ndi amasiye. Alibe mwamuna, ndipo banja lonse likuyangana kwa iye kuti alidyetse. Alibe kothawira chifukwa boma ati lidasiya kuwathandiza. +Mayiyu ndi mmodzi mwa anthu 16 100 amene adatsakamira pachilumba cha Makhanga mboma la Nsanje kwa T/A Mlolo kumayambiriro a chaka chino kaamba ka ngozi ya kusefulira kwa mtsinje wa Ruo. +Madzi osefukirawo pa 12 January 2015, adaphotchola njira nkusiya anthu a midzi isanu ndi iwiri mwa gulupu Sambani ndi magulupu ena pakachilumba ndipo mpaka pano akukhalabe pomwepo kusowa kopita. +Pachilumbapo pali msika wa Admarc, chipatala cha Makhanga, Makhanga CDSS ndi sukulu ya pulaimale. Anthuwa kuti alandire thandizo zikuvuta chifukwa azunguliridwa ndi mtsinjewu. +Anthu a midzi 11 ya mwa gulupu Manyowa ndi Osiyana ndi omwe boma lidakwanitsa kuwasamutsa kukawasiya malo ena, komabe ophunzira amaolokabe mtsinjewo pangalawa kupita kuchilumbako kutsatira sukulu Makhanga CDSS. +Monga akunenera Zakeyu, boma lidawalonjeza anthu otsalawo kuti awasakira kokakhala koma mpaka lero kuli chuuu! Tikudikira lonjezo la boma. Panopa tikafuna msika wa Admarc, chipatala kapena zinthu zina timayenera tioloke mtsinje wa Ruo. +Ngakhale tili ndi sukulu komanso chipatala, palibe zipangizo zokwanira. Tikubwerera kuchipatalako chifukwa chosowa mankhwala. Chimanga chidasiya kalekale kubwera pa Admarc ya Makhanga chifukwa cha mavuto a mayendedwe. Izi zikupangitsa kuti tizilowera mdziko la Mozambique tikafuna thandizo, apo ayi, kuoloka Ruo kupita kumsika wa Osiyana, adatero Zakeyu. +Gulupu Osiyana akuti ngati madzi osefulira angabwere lero, pali mantha kuti midziyi ingathe kukokoloka. +Anthuwatu ali pakati pa madzi. Kungoti mvula yoopsa yagwa lero ndiye kuti anthuwa titayanso, adatero Osiyana. +Iye akuti ngakhale midzi yake ili idaolotsedwa kupita tsidya linalo, ana alibe koti akaphunzire kupatula kupitbe kuchilumbako. +Tilibe sekondale, moti ana athu akumakaphunzira ku Makhanga CDSS yomwe ili pachilumbapo. Sukuluyonso ili ndi mavuto ambiri chifukwa thandizo silifika, adatero Osiyana. +Pamene kwangotsala miyezi iwiri kuti mvula iyambe, boma likuyenera kuolotsa anthuwa, apo ayi, likuyenera kuchita chotheka kuti mtsinje wa Ruo utenge njira yake yakale. +Nthambi yoona za kusintha kwa nyengo ya Climate Change and Meteorogical Services yalosera kuti chaka chino madzi angathenso kusefukira chifukwa mayendedwe a mpweya akusonyeza kuti mvula ingagwe moposera mlingo wake, maka kumalo okwera. +Koma mneneri wa nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi ya Department of Disaster Management Affairs (Dodma), Jeremiah Mphande akuti ntchito yosamutsa anthuwa iyamba posachedwapa. +Iye wati padakalipano nthambi yawo yalemba ntchito kampani ina yomwe ikuyeza momwe angathanirane ndi vutoli. +Chomwe tikufuna ndi kupanga mulambala kuti mtsinjewu ubwerere komwe umadutsa chifukwa pali mtunda wa makilomita 7 kuchokera komwe ankadutsa poyamba. +Pakutha pa miyezi iwiri, atiuza zomwe apeza ndipo tikatero tiyamba kusaka ndalama zoti zithandizire ntchitoyi, adatero Mphande. +Iye adati ntchitoyi yachedwa chifukwa ngoziyi idachitika ndondomeko ya zachuma ya boma itadutsa kale. +Panopa ndiye kuti pakufunika ndalama zapadera kuti ntchitoyi igwiridwe, adatero. +Kodi anthu adikire izi? Mphande adati padakalipano anthuwo akuyenera asamuke poopetsa ngozi ina ngati mvula ingagwe msanga. +Kutambasula unamwali wa mtete Nyazgambo kuonetsa momwe ankavinira Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndakupezani kuno ku Embangweni. Tatiuzeni zambiri za mtete. +Mtete ndi unamwali womwe kalelo ankatilangira. Ankatitsekera mkachipinda komata kwa sabata imodzi kwinaku akutiphunzitsa zambiri zoyenera kuchita tikadzakwatiwa. +Talongosolani bwinotu pamenepo? Mwa zina ankatiphunzitsa magwiridwe a ntchito tikamacheza ndi abambo. Apatu nkuti tikuimbira kanyimbo: Ko! Kokoliko! Ko! Kokoliko! Tambala walira ayiye timpatse malango! Nyimbo imeneyi timavina titamangira nsalu mchiunomu. Nsaluyi imathandizira guleyu. +Nchifukwa chani adakuphunzitsani kuvina mtete? Nyazgambo kuonetsa momwe ankavinira Ine adandiuza kuti ndizivina mtete chifukwa ndikapita ku banja opanda mtete, mwamuna akandisiya. Ndiye iii! tinkamvera ndi chidwi kwambiri kuti potha pa sabatayi tikhale titadziwa kuvinako komanso titamva mwambo wonse omwe agogo adali kutilangiza. Agogowa ankatiphunzitsa kuvinaku tsiku lililonse. +Tidakhala sabata yatunthu tili mnyumba pamenepo anzathu adali kusukulu. +Ankati mwamuna akakusiyani chifukwa chiyani? Akuluakulu ankati popanda mtete, basi mwamuna akapeza wina ndipo ankatiphunzitsiratu zoyenera kuchita. +Palinso china chomwe mudaphunzira? Eya, ankawalanganso atsikana amwano ku unamwali omwewu. Amawaveka chitenje atachimanga ngati kabudula, akuvina namazungulira ndi matakowa. Kwinaku akutchula za mwano zonse zomwe amawachitira makolo awo. +Kodi unamwaliwu udathandizirapo kuti mudye mfulumira, ndi cholinga chokachita zomwe mudaphunzirazo? Kumbali yanga ayi ndithu, chifukwa alangizi ankaneneratu kuti tidzisunge mpaka tsiku lodzalowa mbanja. Komabe ndikudziwa atsikana anzanga omwe adatenga mimba chifukwa chofuna kuyeserera zomwe tidaphunzira zija. +Nde mwati amalanganso atsikana amwano komweko? Nthawi zina makolo amatumiza ana awo ku unamwaliwu akakhala nkhutukumve. Awa amakhala atsikana wosatumikira makolo. Uku ndiye kumakhala kulangidwa, mbali inayi monga ndanena kale akuvina mokhwekhwereza matakowa. Apatu ndiye kuti agogo akulandizana nyimbo kwinaku akuwaitana maina awo, nkumatchula za mwano zomwe amawachitira makolo awo. +Mwachitsanzo chabe ankati: Jane katunge madzi ku dambo ndipo woyankhira ankati ayi sindikufuna. +Kodi izi zimathandiza kuthetsa mwanowo? Zimathandiza chifukwa amatuluka osinthika ndithu. Mwano uja umathera komweko. +Kodi padali zomuyenereza mtsikana kulowa ku unamwali umenewu? Unamwaliwu amalowa ndi mtsikana wotha msinkhu. Sikumalowa ana. Koma zaka 12 kupita mtsogolo ndipo akhale woti wagwa mdothi. +Nanga tsiku lotuluka likakwana, ndi malangizo anji omwe mudali kulandira? Akuluakulu adali kutilangiza kuti tisakasiye kuvina mtete kuti tikazolowere (Mtete uwu mungalekenge cha kuvina). +Kodi zidakuthandizani? Pamenepa ndingangoti, ndimadziwa ndithu. +Kodi unamwaliwu ukadalipo? Ayi ndithu. unamwaliwu udatha kaamba kakubwera kwa amabungwe ophunzitsa za maufulu osiyanasiyana komanso olimbikitsa kuti atsikana asamathamangire kukwatiwa koma azilimbikira sukulu. Adatiuza kuti kudali kolakwika kuchita izi chifukwa anawa adali kujomba kusukulu kwa sabata yatunthu zomwe zimasokoneza maphunziro awo. Komanso adati ndi zina mwa zomwe zimalimbikitsa ana akazi kulekeza sukulu panjira ndi kukwatiwa msanga. +Kwezani ndalama ku umoyoMHEN Mavuto a zaumoyo mMalawi muno ndiye ndi osayamba. Odwala kuthinana mzipatala, mankhwala kusowa, madotolo ochepa komanso zipatala zotalikana. Mkulu wa bungwe la Malawi Health Equity Network (Mhen) George Jobe, wati mavuto onsewa akudza chifukwa dziko lino silikuyika K15 ya K100 ya ndondomeko ya zachuma ku ntchito zaumoyo. +Jobe adati maiko a mu Africa kuphatikizapo Malawi adasainira pangano ku Abuja mu 2001 kuti ndalama zoika ku zaumoyo zisamachepere K15 pa K100 iliyonse. Maiko adasayinira panganolo limene adalilimbikitsa ndi a bungwe loona zaumoyo padziko lonse la World Health Oragnisation (WHO). +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mzipatala zina mumakhala kuthinana kwambiri Kafukufuku wa Tamvani, wasonyeza kuti zaka zitatu zapitazi, ndondomeko ya zachuma mdziko muno yakhala ikupereka ndalama zosaposa K8.70 pa K100 iliyonse ndipo pandondomeko imene tikuyendera pano kudayikidwa ndalama zochepetsetsa kuposa zaka zonse. +Jobe adati izi zikudzetsa mavuto a kusowa kwa mayendedwe (ma ambulansi), chiwerengero cha ogwira ntchito, kutalikana kwa zipatala ndi kusowa mankhwala. +Amene adaphunzira ntchito za chipatala ambiri akusowa ntchito, adatero Jobe. +Iye adati pmaiko adagwirizananso kuti pamayenera kukhala makilomita 8 kuchoka pachipatala china kukafika china ndipo posachedwapa mtundawu udatsitsidwa kufika pa makilomita 5 koma dziko la Malawi silikwanitsabe. +Komanso misewu yake ndi yomvetsa chisoni zomwe zimakhudzanso nkhani ya mayendedwe. Ma ambulansi ndi osowa mzipatala ndipo akapezeka, umva kuti palibe mafuta, adatero iye. +Iye adati vuto lalikulu ndi kasamalidwe ndi kayendetsedwe ka ntchito poyeza ndi kupereka mankhwala kwa odwala. +Mankhwala ena boma limagula koma ena makamaka okhudzana ndi malungo amachokera kwa maiko otithandiza omwe ali ndi malamulo awo, adatero iye. +Iye adati athandiziwo akapereka mankhwalawo amereka limodzi ndi zida zoyezera ndiye nthawi zina chifukwa chochuluka kwa odwala, a chipatala ena sayeza, amangogwiritsa ntchito zizindikiro. +Adaonjeza: Akabwera otithandiza, amapeza kuti mankhwala atha, koma zoyezera zikadalipo tsono amavuta kuti apereke mankhwala ena msanga. +Mneneri wa unduna wa zaumoyo Andrian Chikumbe adalephera kupereka ndemanga pa nkhaniyi Tamvani atamugogodera kuyambira Lachiwiri. +Mneneri wa unduna wa zachuma, Alfred Kutengule, adati boma la Malawi limalephera kukwaniritsa zinthu zina chifukwa chakuchepekedwa. +Chilungamo nchakuti mapezedwe athu ngovutirapo. Timayenera kukambirana ndi anzathu otolera misonkho kuti tiwone momwe tingagawire kochepa komwe atolelako nchifukwa chake zina timalephera, adatero Kutengule. +Izi zili choncho, Amalawi ndi amene akusautsika kwambiri, patatha zaka zoposa 50 chilandirire ufulu wathu. +Ena mwa anthu amene tidacheza nawo adandaula za kuthinana kuchipatala, kusowa mankhwala, kuyenda mtunda wautali ngati ena mwa mavuto amene amakumana nawo. +Ulova wafika posauzana Adatenga digiri ya uphunzitsi mu 2010 ku Chancellor College (Chanco), kaamba kosowa ntchito, tsopano wachoka mtauni ndipo akukhala kumudzi komwe akusaka timaganyu. +Chiyembekezo cha ntchito chidadza pa 23 July 2016 pamene bungwe la Global Warming Research International (GWRI) lidalengeza mwayi wa ntchito pokhoma mauthenga mmitengo ku Dedza. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Osaka ntchito mazanamazana kuyesera mwayi wawo ku Golden Peacock mumzinda wa Lilongwe mmboyomu Wolemba Udali mwayi wa nzama kwa Joackim Nyanda pomwe bungweli limafuna amene ali ndi pepala la JCE ndipo amene ali ndi loposera apa akhala ndi mwayi waukulu kupeza ntchitoyo. +Ndi mtima wonse, Nyanda, wa zaka 30, adakhulupirira kuti mwayi wa ntchito aupeza chifukwa cha digiri yomwe akusunga. Akadadziwa akadaphika therere. Sudali mwayi koma tsoka chifukwa bungwelo lidamuyeretsa mmaso pomubera ndalama dzuwa likuswa mtengo. +Izi ndizo zikuchitika mmaboma a Dedza, Ntcheu, Mangochi komanso Kasungu komwe anthu akulira ndi bungwe la GWRI powanamiza kuti awapatsa mwayi wa ntchito, malinga ndi anthu komanso apolisi amene talankhula nawo. +Kudakhomedwa uthenga mmitengo kuti bungweli likufuna anthu oti awerengere chiwerengero cha anthu mdziko muno. Amati tilembere kudzera pa E-mail kapena kutumiza uthenga pafoni. +Udali mwayi wanga, ndidatumiza kudzera pafoni chifukwa E-mail imabwerera. Nditatumiza, adandiyankha kuti athokoza potumiza uthengawo ndipo adati nditumize K1 000 kumpamba pa 0882 453 891 yomwe idzagwiritsidwe ntchito pogulira chakudya tsiku lomwe adzatiitanelo, adatero Nyanda, yemwe ali ndi mwana mmodzi ndipo akukhala ku Dedza. +Uthengawo, womwe Tamvani yauona, udati anthu amwayi adzaitanidwa kuti akakumane kuholo ya Umbwi Secondary School pa 25 ndi 26 July nthawi ya 9 koloko mmawa. +Uthengawo udatinso amene adzachite mphumi adzapatsidwa ntchito yochita kalembera amene achitike miyezi isanu mmaboma a Lilongwe, Karonga, Nkhotakota, Salima, Ntcheu ndi Dedza ndipo ntchitoyi idzagwiridwa mzigawo. +Poyanganira ulova womwe wachuluka mdziko muno, anthu pafupifupi 100 akuti adakakumana kuholo ya Umbwi pa 25 July zomwe zidadabwitsa mphunzitsi wamkulu pasukuluyi. +Mphunzitsiyu, Alick Mnzanga, adati iye adangodabwa anthu akusonkhana pasukulupo. +Choyamba nditaona uthengawo, ndidaimba nambala yomwe idali pauthengawo chifukwa chomwe akulembera zoti adzakumana kuno pamene adali asadadzatidziwitse. +Adandiyankha kuti abwera koma sadabwere, kenaka tidangodabwa anthu akutulukira. Titaimbanso nambalayo simapezeka ndiye ndidawauza anthuwo kuti abwerere, adatero mphunzitsiyu. +Apa mpamene Nyanda limodzi ndi anzake adadziwa kuti aberedwa. Loto lopeza mwayi wa ntchito kwa Nyanda lidasandukanso la chumba. +Si ku Dedza kokha komwe aona zoterezi, nakoso ku Ntcheu, Mangochi ndi Kasungu akuti ena awakwangwanula masanasana mdzina lopeza mwayi wa ntchito. +Gift Bengo wa mmudzi mwa Zakutchire kwa T/A Champiti ku Ntcheu nayenso adamubera mnjira yotereyi. +Sindigwira ntchito koma ndili ndi pepala la Fomu 4. Nditaona uthengawo, ndidangoti mwayi wangawo. +Adati tikakumane ku holo ya New Era, umo mudali mu June, ndipo tidakakumana anthu pafupifupi 200 komwe tidauzidwa ndi eni sukuluyo kuti sakudziwa chilichonse ndipo manambalawo samagwiranso, adatero. +Naye mneneri wa polisi ya Mangochi, Rodrick Maida, akuti kumeneko zidachitika mwezi wathawu ndipo amauzidwa kuti akakumane kusekondale ya Mangochi. +Koma anthuwo amene adalipo pafupifupi 80 atakakumana kusukuluko, adabwezedwako kuti sakudziwa chilichonse cha nkhaniyo. +Panopa apolisi tikufufuza za nkhaniyi, koma vuto ndi loti manambala awo sakupezekanso zomwe zikupangitsa kuti kafukufuku wathu avute, adatero Maida. +Tamvani atayesera kuimba pa nambala ya 0991 743 325 yomwe bungweli limati anthu azitumizirako uthenga wofunsira ntchito, sidapezeke mpaka pamene timalemba nkhaniyi. +Nayo nambala yomwe amati azitumizirako K1 000 ku Mpamba simapezeka. Titafufuzanso pa Google ngati bungwe la Global Warming Research International lilipo, palibe zotsatira zomwe tidapezapo. +Kodi bungwe loona zofalitsa mauthenga la silingathandizepo kupeza amene wawachita chipongwe anthuwa? Mneneri wa bungwe la Malawi Communications Regulatory Authority (Macra), Clara Mwafulirwa, adati woyenera kuyankhapo pankhaniyi ndi a TNM osati iwo. +Ukamatsegula Mpamba, umayenera ukhale ndi chiphaso chako kusonyeza kuti uthenga wonse umayenera upereke. Tafunsani a TNM amene angayankhepo, adatero. +Mneneri wa kampani ya TNM, Limbani Msapato, adati sakufuna kulankhulapo pankhaniyi. Momwe mukufotokozeramo nzovuta kuti ndilankhulepo, adatero iye. Koma Titamupempha kuti awalangiza zotani omwe amagwiritsa ntchito mafoni a TNM, iye adati: Sindikufuna kulankhulapo, dikirani ndiimbanso. Koma sadaimbe kufikira nthawi yosindikiza nkhaniyi. +Malinga ndi bungwe la kafukufuku wa ziwerengero mdziko muno la National Statistical Office (NSO) za 2014, anthu 8 mwa 10 alionse mdziko muno sali pantchito yolembedwa. +Nduna ya zachuma, Goodall Gondwe, polankhula nthawi yomwe Nyumba ya Malamulo imakumana, adati malinga ndi mavuto a zachuma, boma lizingolemba apolisi, asirikali ndi anamwino. +Posakhalitsapa, khamu la anthu lidasonkhana ku Golden Peacock mumzinda wa Lilongwe komwe ankafuna kulemba antchito owerengeka chabe koma zidadabwitsa pamene anthu miyandamiyanda adasonkhana mmizere yaitali kufuna kuyesa nawo mwayi wa ntchitowo. +Chisangalalo chafika, Samalani kuli mavuto Mawa laliwisiri ndi tsiku la Khirisimasi ndipo Lamulungu sabata ya mawa ndi tsiku lokumbukira kulowa chaka cha 2017. Iyi ndi nthawi imene ena amasangalala ngati kulibe mawa, koma akadaulo anenetsa kuti iyi ndi nthawi yokumbukiranso kuti kuli msilikali wamkulumwezi wa Januaryamene amasiya ambiri mmatumba muli mbeee! Ena amavulala kapena kufa kumene chifukwa chosangalala mosasamala. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Katswiri pa zachuma, Henry Kachaje, wati matumba amabooka mu January chifukwa cha kusakaza ndalama mosasamala nyengo ya zikondwereroyi. +Iye adati ndondomeko yabwino pakagwiritsidwe ntchito ka ndalama ingathandize kupeputsa ena mwa mavuto omwe amaoneka mu January monga ngongole zosakonzekera. +Anthu adali pakalikiliki kugula katundu msabatayi Iyi ndi nthawi yomwe timaona anthu akumwa, kudya ngakhalenso kuvala moposa mapezedwe awo. Mchitidwewu ndiwo umabala mavuto mwezi wa January, adatero Kachaje. +Iye adati kukonzekera kwa nzeru nkuonetsetsa kuti zinthu zofunikira kwambiri monga chakudya zagulidwa mokwanira nkusungidwa moyenera mapwando asadayambe. +Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe olimbikitsa maphunziro la Civil Society Coalition for Quality Education, Benedicto Kondowe, adati ana ena alephera kupita ku sukulu chifukwa choti makolo awo adaononga ndalama za fizi. +Kondowe adati pomwe makolo akukonza zisangalalo zosiyanasiyana, alingalirenso za ndalama za fizi ya ana awo kuti asadzagwire njakata nthawi yotsegulira sukulu ikadzafika. +Chowawa kwambiri pamoyo wa mwana nkuona anzake akupita kusukulu iye ali pakhomo kaamba kosowa fizi. Kuli bwino kuchepetsa chisangalalo koma nthawi ikafika, ana adzapite kusukulu, adatero Kondowe. +Mkulu wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) Prince Kapondamgaga adati kusangalala nkofunika pamoyo wa munthu koma adachenjeza alimi kuti asaiwale kugula zipangizo zaulimi kaamba kokomedwa ndi zisangalalo. +Iye adati mlimi wanzeru amaonetsetsa kuti chilichonse chomwe angafune paulimi wake chilipo asadayambe kulingalira zina chifukwa iyi ndiyo njira yomwe iye angapindule nayo paulimi wake. +Aliyense amafuna kusangalala mmoyo mwake koma zinthu zimakoma zikamayenda ndi nthawi komanso kuthekera komwe kulipo. Osayamba maphwando ulibe zipangizo zaulimi ngati ndiwe mlimi, adatero Kapondamgaga. +Mkulu wa bungwe loyanganira za anthu ogula la Consumers association of Malawi (Cama) John Kapito adati anthu asaiwale za njala yomwe iliko chaka chino. +Iye adati nzopanda phindu kusangalala masiku ochepa koma kenako nkudzavutika masiku ambiri ndi njala zomwenso adati zingapangitse chitukuko kulowa pansi. +Tonse timadziwa kuti munthu amagwira bwino ntchito ndi mkhuto ndiye ndi njala ya chaka chinoyi, nkofunika kusamala kwambiri pa momwe tingakonzere zisangalalo zathu. Tiyeni tionetsetse kuti tasungako ndalama ndi chakudya mmakomomu, adatero Kapito. +Mchikalata chake mnyengoyi, bungwe loonetsetsa kuti malonda akuyenda mokomera aliyense mdziko muno la Competition and Fair Trading Commission (CFTC) lati nyengo ngati iyi amalonda ena amafuna kukokera ponyenga ogula. +Bungweli lati nyengoyi, anthu a mabizinesi amagwiritsa ntchito bodza potsatsa malonda awo ndi cholinga choti anthu akopeke ndipo kawirikawiri anthu sazindikira kuti apusitsidwa kaamba kakukomedwa. +Ambiri amanama kuti atsitsa mitengo. Mwachitsanzo, amatha kunena kuti katundu wafika pa K15 000 kuchoka pa K25, 000 chonsecho katunduyo sanagulitsidweko pa K25, 000, lidatero bungwelo. +Alimi samalani pososa Mlimi weniweni ndiye amasamalitsa kalendala yake ya ulimi. Kuyambira mwezi watha mpaka uno, alimi amalangizidwa kuti akuyenera kuyamba kusosa. +Mlangizi wamkulu mboma la Chiradzulu, Sheila Kangombe wati alimiwa ayenera asamalitse pamene akusosa chifukwa chiyambi chosakolola zochuluka ndi nthawi yososa. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kangombe adati alimi akuyenera kudziwa kuti mitengo ya thonje ndi fodya siyiyenera kukwiriridwa chifukwa nthawi zambiri imakhala ndi matenda. +Pofotokozapo njira zabwino za kasosedwe, Kangombe adati kukwirira mapesi ndi ndondomeko yabwino ya kasosedwe chifukwa kumasunga manyowa. +Alimi angathe kukwirira mapesi ngati awa Mapesi a chimanga mtedza ndi mbewu zina ayenera akwiriridwe, iyi ndi njira yabwino ya kasosedwe chifukwa zikaolerana zimapanga manyowa. +Ena amakonda kuotcha mapesi, izi siziloledwa koma mitengo ya fodya ndi thonje ndi zomwe ziyenera kuotchedwa. Mapesi achimanga komanso mbewu zina amabweretsa manyowa ngati akwiriridwa, adatero iye. +Madera ambiri alimi ayamba kale kukwirira koma ena sadayambe monga zilili ku Dedza komwe alimi ali otangwanika ndi kukumba kachewere ndi mbatata ya kholowa. +Sylvester Chitini wa mmudzi mwa Salile kwa T/A Kasumbu mboma la Dedza akuti kumeneko alimi sadayambe kusosa komabe mwezi ukudzawu ayambapo. +Pano ndife otangwanika ndi kukumba mbatata ya kholowa komanso kachewere. Nthawi zonse timayamba mochedwa kusosa kuno. Kumapeto kwa September aliyense akhala wayambapo kusosa, adatero iye. +Mboma la Blantyre ndi maboma ena alimi ena akumaliza kusosa pamene ena akuyamba kumene. Tomasi Kandodo wa ku Chilomoni akuti sabata ikubwerayi akhala atamaliza kusosa munda wake. +Apempha mafumu kuunika miyambo Boma komanso nthambi ya mgwirizano wamaiko wa European Union (EU) atsindika kufunika koti mafumu aunikenso miyambo ina yomwe ikadatsatidwa mzigawo zosiyanasiyana mdziko muno. +Mfundo iyi ndiyo idatenga gawo lalikulu la msonkhano wa masiku awiri msabata yangothayi wa mafumu akuluakulu ku Golden Peacock mumzinda wa Lilongwe. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Lukwa: Miyambo ina isinthe Cholinga cha msonkhanowo chidali chofuna kupereka mpata kwa mafumuwa kukambirana za malamulo omwe mafumu amatsata poyendetsa zinthu mmadera mwawo koma kudaoneka kuti milandu yambiri yomwe imafuna malamulowa imakhudzana ndi miyambo. +Nduna yoona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa abambo, amayi, anyamata ndi asungwana Jean Kalirani adanena motsindika kuti amai ndi ana ambiri amachitiridwa nkhanza zikuluzikulu kaamba kofuna kukwaniritsa miyambo ina. +Nzoona kuti mpaka pano tizikhala tikukamba za miyambo monga kulowakufa, kuchotsa fumbi, phwando la nkhandwe ndi fisi? Zonsezi zikuchitika mmadera momwe mafumu amakhala ndipo ali ndi mphamvu zosintha zinthu, adatero Kalirani. +Iye adati Malawi ngati dziko limodzi lomwe lidalowa nawo mumgwirizano wa maiko, ali ndi udindo oonetsetsa kuti zomwe maikowo adagwirizana zikutsatidwa ndipo chimodzi mwa mapanganowo nkuonetsetsa kuti nkhanza kwa amai ndi ana zatha. +Woimira bungwe la United Nations (UN) Ama Sande adati iye ndi nthumwi zina za kunthambi ya amayi mu mgwirizano maiko a dziko la pansiwu adagwidwa ndi chisoni atayendera madera ena nkupeza asungwana achichepere omwe adawafotokozera za momwe amakakamiziridwa kugonana ndi akuluakulu. +Iye adati adakhudzidwa kwambiri akuluakulu ena omwe adacheza nawo atawayankha poyerayera kuti mwana ndi wa zaka 8 koma akafika zaka 12 ndiye kuti wakula. +Chomvetsa chisoni kwambiri nchakuti zambiri mwa nkhanza zomwe asungwana adafotokoza zimachitika kaamba ka miyambo yomwe imatsatidwa mmadera awo, adatero Sande. +Senior Chief Lukwa ya ku Kasungu idati zomwe adanena akuluakuluwa nzoona ndipo adalonjeza kuti pamsonkhanowo mafumu akambirana za mfundo zokhwima zotetezera amayi ndi ana chifukwa chamiyambo. +Iye adati kuti izi zitheke nkofunika kuganizira mafumu pankhani yamayendedwe komanso ndalama zogwirira ntchito yawo mosavuta chifukwa nthawi zambiri amalephera kufikira anthu omwe akuzunzika kaamba kosowa pogwira. +Woyanganira zakayendetsedwe ka ntchito kuunduna wa maboma angonoangono Norman Mwambakulu adalimbikitsa mafumuwo kuti ali ndi mphamvu zopanga malamulo omwe Nyumba ya Malamulo ikhoza kungovomereza. +Koma pa Wenela zidzatheka? Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Tsikulo tidakhala pa Wenela. Tidali kusowa cholankhula. Kodi ndi January ameneyu? Ayi ndithu. Kukazinga chimanga chisanachoke mmunda. +Nyimbo zomwe ankaika Gervazzio tsikulo palibe icho ndinkatolapo. Mvula idali ikugwa. +Wamkana ku Europe! Wamkana ku America! Wamkana mwana wake! Iyinso nyimbo idali kuphulika pomwe tidamva kuti ndege zidali kutera pa Wenela. Pajatu pa Wenela pali bwalo la ndege. +Tidangomva mkokomo wa ndege. +Timayesa ikutera. +Inkatera. +Koma siyidali ndege. +Lidali lichero. +Tonse tidathawa! Licherolo mudali Joloji Chadyaka yemwe ena amayembekezera kuti afikira ku Lumbadzi. Koma abale anzanga, ngati kuli munthu amene ndimadabwa naye, ndiye ndi ameneyu. +Nanga inu, munthu anganene za kutsitsa mpweya nkumatsika lichero pa Wenela mungadabwe nazo? Komatu nkokomo umene unkamveka pa Wenela aliyense adathawa. +Tsono. Tsono. Tsono. +Sindinadabwe ndi za Chadyaka. Chadyaka ndi Chadyaka basi kaya munena za mmera, kaya soya, kaya nsetanyani, kaya thonje. Chadyaka ndi chadyaka basi! Ndimamukumbuka mkulu ameneyu. +Adayenera kufika ku ukwati wa mwana wa mnzanga 2 koloko. Mwambowo umayenera kutha 4 koloko. Iye adafika 4:20pm. +Inetu zonena zambiri ndilibe. +Ndiye mwati anthu otchuka atatu anabwera pa Wenela nthawi imodzi? Mwati uyu Dona adatenga Melise ndi Davide anafika pa dambwe lathu ku Kumbali wafika mdziko muno kudzatenga ana ena? Bwanji osatenga nkhalamba ya chibwana Joloji Chadyaka? Bwanji osatenga Moya Pete? Ndiye mwati kwafikanso uyu Rihhhhon? Pakadakhala kuti Abiti Patuma alipo nkadamufunsa, koma anali atapita kofufuza nkhanizo. Pa Wenela panalibepo. +Ndinkamphunzitsa kuimba gitala Pa 29 October chaka chino, anthu mumzinda wa Lilongwe adaona zachilendo pamene mkwati ndi mkwatibwi adakwera chitharakitale chokonza misewu osati Benz monga ambiri amachitira. Uwutu udali ukwati wa Sally Nyundo, katakwe woimba chamba cha Reggae, ndi Tionge Kalua. Nyundo adatchuka kwambiri ndi nyimbo yake yotchedwea Ras amadya nzimbe. +Ukwatiwutu adadalitsira pampingo wa Lilongwe Pentecostal pomwe madyerero adali ku Louis Garderns ku Area 3 mumzinda womwewu wa Lilongwe. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Nyundo ndi mkazi wake Nyundotu akuti adakumana ndi mkazi wake Tionge panthawi yomwe njoleyi inkafuna kuphunzira kusewera gitala. +Iye adati Annie Matumbi,naye mmodzi mwa oimba kuno ku Malawi, ndiye adauza Tionge kuti Nyundo ndi kadaulo pa nkhani za magitala ndipo akhoza kumuphunzitsa bwino lomwe. +Ndinamuuza Matumbi kuti ampatse nambala yanga tilumikizane. Tidalankhulana pafoni ndipo adaguladi gitala. Apapatu nkuti tisadakumanepo. Tidakumana pa Cross Roads mumzinda wa Lilongwe kuti tiuzane za maphunziro a gitala, adalongosola motero Nyundo. +Iye adati komatu maphunziro amayenda mwamanyazi chifukwa aliyense adali ndi mawu kukhosi koma amasowa woyambitsa. +Malinga ndi Nyundo, mmanyazimu mudautsa kachikondi kanchibisira. +Ndidakopeka naye mtima chifukwa adali munthu wodekha, wozichepetsa komanso maonekedwe ake okongola, iye adatero. +Koma pajatu naye mkazi amakhala nayo mbali yake yomwe amakopedwera ndi mwamuna, ndipo kwa Tionge, adakopeka ndi kudzichepetsa komanso kucheza bwino ndi anthu kwa Nyundo. +Tidadziwana bwino lomwe ndipo aliyense adali wofunitsitsa kumanga banja, Nyundo adalongosola. +Awiriwatu adakhala paubwenzi kwa zaka zitatu ndipo akumana ndi zovuta monga zokambakamba zambiri zochoka kwa anthu omwe samawafunira zabwino, komatu sadazitengere izi, adamasukirana ndi kumvetsetsana. +Tidatseka makutu, nthawi zomwe tinkakumbutsana za chikondi chathu. Ndipo akazi anga nthawi zonse ankandilembera timakalata tachikondi takupulaimale monga ta kiss to kiss ndi love to love, zomwe zinkakometsa chikondi chathu. Komanso tinkakhala ndi nthawi yambiri yopita ku picnic kukacheza, adatero Nyundo. +Mwambo wa ukwati wa Chitonga Mtundu wina uliwonse uli ndi chikhalidwe chake. Ndipo nawo mtundu wa Atonga womwe umapezeka kwambiri ku Nkhata Bay ndi Nkhotakota uli ndi mwambo wawo wa ukwati. Masiku apitawa Martha Chirambo adacheza ndi MfumuVimaso yochokera mdera la T/A Kabunduli ku Nkhata Bay ndipo idalongosola za mwambowu motere: Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Takupezani gogo. Ifetu timafuna timve zambiri za mwambo wa ukwati wa Chitonga. +Ife Atonga monga mtundu wina uliwonse tili ndi dongosolo lathu lomwe timatsatira panthawi ya ukwati. Sitimafuna ukwati wa mnjira. +Vimaso kulongosola za mwambowu Tatambasulani kuchokera pachiyambi. Zimatani mkazi wa Chitonga akapeza bwenzi lomanga nalo banja? Mkazi wa Chitonga weniweni akakumana ndi mwamuna woti akumfunsira banja savomerana kunjira konko, ayi. Mwamunayu pamodzi ndi mnzake amafika pakhomo pa namwaliyo kudzafunsira. Ndipo pofunsirapo namwaliyo pamakhala palibe, amafunsira agogo ake kapena achemwali ake. Awa ndi omwe amakamfunsanso namwaliyo kumbali. Mtsikanayo akavomereza, mwamunayo amapereka chikole mwina K200 000 kapena molingana ndi mapezedwe ake. Ndalama imeneyi imadzagwiritsidwa ntchito yogulira ziwiya panthawi ya ukwati. Apanso ndi pomwe mwamunayo amafunsa khomo lokafikira thenga pochita dongosolo lomanga banja. +Pamakhalanso dongosolo lina? Eya, limakhalapo. Akwawo kwa mwamuna tsopano amafikanso pamudzipo kudzadziwitsa anthu kuti tambala wawo wapeza msoti pakhomopo. Apatu samangobwera chimanjamanja, ayi, amanyamulanso ndalama yomwe timaitchula kuti chiziyapamuzi ndipo zokambirana zimayamba tsopano. Anthuwa akagwirizana, ndi pomwe amapereka malowolo. Zikatero ndipomwe amapempha za tsiku la ukwati. +Koma ndiye zolowa zikuchulukatu! Apanso amakhala asanamalize chifukwa amaperekanso mkhuzi. Ili ndi bulangete lomwe limaperekedwa kwa make mwana. Komatu silimakhala bulangete wamba, ayi. Chimakhala chibulangete chenicheni. +Kodi patsiku la ukwati, zimakhala bwanji? Pakatsala masiku awiri tsikuli lisadafike, akuchikazi amakatula nkhuni kuchimuna. Izi zimakhala zodzaphikira patsiku la ukwati komanso zina zoti akamusiyire namwaliyo. Ndipo kukatsala tsiku limodzi amakatula ufa wambirinso, nyama komanso ziwiya zophikira. Ukwati ukachitika, amayi ena pangono amatsalira ndipo amaphika zakudya zambiri ndi kupereka kwa abale a mwamuna. Izitu zimachitika ngati njira yowauzira kuti pamudzipo pafika mkazi watsopano. +Izi zikadutsa, amayiwa amabwerera mmbuyo. +Kodi palinso mwambo wina kapena zikafika apa basi zatha? Amayi anayi tsopano amalowa mbwalo. Awiri akuchikazi komanso awiri akuchimuna omwe timawatchula kuti azamba amnyumba. Ntchito ya awa ndi kuwaphunzitsa awiriwa zenizeni za banja tsopano. +Apatu ndi pamene akuluakulu amadziwiranso ngati mwamuna ali wobereka kapena ayi, komanso ngati mkazi anali woyendayenda. +Ndi zothekadi zimenezi? Awiriwa amapatsidwa tinsalu tiwiri togwiritsa ntchito akamaliza kugwira ntchito komanso kamphika ka madzi. Ndipo macheza akatha, azambawa amaona tinsaluto ngati mwamunayo ali wobereka kapena ayi mwaluso lawo. +Chimachitika ndi chiyani akapezeka kuti ngosabereka? Ngakhale apezeke kuti sizidayende, azambawa saulula, chimakhala chinsinsi chawo. +Kodi amaunikidwa ndi mwamuna yekhayo? Nanga mkaziyo? Naye mkazi ali ndi zake zomwe amamuunika. Makamaka amaunika ngati ali woti sanagonepo ndi mwamuna wina. Ndipo akapezeka zonse zili bwino, mwamunayo amalipira ndalama ndithu. +Akapezeka kuti izi zidachitikapo, zimamuthera bwanji? Akuluakuluwa amakhumudwa kuti wawachititsa manyazi, komanso mwamunayo sapereka ndalama ija. Kwambirinso akuluakuluwa amakhumudwa kuti mwana wawoyo sadaulule kuti kunayendako munthu wina. Akaulula ukwati usadachitike, amapatsidwa mankhwala ndipo amakhalanso ngati wanyuwani. Amabwerera mchimake bwinobwino ndithu. +Kodi zikuchitikabe? Ife akumudzi timachitabe izi pomwe amtauni adaiwalako zotsatira mwambo ndipo akamakwatirana amakhala kuti adathana kalekale. +Kunyalanyaza kudzetsa ngozi Sabata yangothayi ngozi zidakuta dziko lino pomwe anthu 17 adafa. +Pamene anthu amati akhazikitse mitima pansi, anthu 8 atafa pa ngozi ya basi pamlatho wa Rivirivi ku Ntcheu komanso anthu 4 adamwalira ku Bunda ku Lilongwe ndi 4 kwa Magalasi mumzinda wa Blantyre, Lachisanu kudalinso ngozi ina mumzinda wa Blantyre pomwe munthu mmodzi adamwalira. Ndipo kudalinso ngozi zina ku Zomba, Mzimba ndi Mulanje. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mneneri wa apolisi James Kadadzera adati ngozi zikuchuluka chifukwa chothamanga kwa madalaivala mosatsata malamulo. +Kadadzera adati madalaivala amakanika kuwongolera galimoto yothamanga kwambiri akadodometsedwa kapena kudzidzimutsidwa pamsewu. +Mwa zina, ngozi ya galimoto yomwe idanyamula simenti ku Blantyre ndi chifukwa chokanika kumanga mabuleki koma nkhani ndi kuthamanganso kosatsata malamulo. Ukalondoloza zikwangwani za pamsewu, ngozi ikachitika sikhala yoopsa chifukwa munthu amatha kuwongolera komanso kupeweka. Vuto anthu akufuna kukafika msanga atanyamuka mochedwa zomwe zikusokoneza kayendedwe pamsewu, adatero Kadadzera. +Iye adapempha okwera mabasi kuletsa madalaivala akamayendetsa galimoto mopanda dongosolo. +Oledzera asaloledwe kuyendetsa galimoto. Akamathamanga kwambiri chonde dziwitsani apolisi mungakumane nawo kuti adzudzule dalaivalayo. Tili tcheru kuonetsetsa kuti malamulo atsatidwe pamsewu popewa ngozi, adatero Kadadzera. +Kaamba ka ngozizo, bungwe la akatswiri a zomangamanga la Malawi Institute of Engineers (MIE) ladzipereka kuthandiza apolisi ndi nthambi zonse za boma zoona za pamsewu kuthana ndi ngozi. +Chikalata chosainidwa ndi mkulu wa MIE Martin Chizalema chidati: Pakuyenera kukhala kafukufuku wozama opeza gwero la kuchuluka kwa ngozi pamsewu. Tiyike mwachangu njira zothana ndi ngozi zoopsazi zomwe zikubwezera chitukuko cha dziko lino mmbuyo. +Chizalema adatinso anthu atenge umwini oteteza miyoyo yawo pa msewu komanso eni galimoto azionetsetsa kuti zili bwino komanso kupewa kuimba lamya akuyendetsa. +Gulewamkulu ndi mankhwala Matenda akagwa pakhomo, makolo amakhala ndi njira zochuluka zothetsera matendawo malinga ndi zikhulupiriro zawo. Ena okhulupirira gulewamkulu akuti ngati mthupi mwabaya, akangovina wodwala amachira pomwepo. Mmudzi mwa Siledi kwa Senior Chief Kanduku mboma la Mwanza muli mayi wina amene ati adachira gulewamkulu atapalasa. BOBBY KABANGO akucheza ndi mkulu wa dambwe kumeneko, Maxwell Kondwerani. +Gulewamkulu akuti ndi mankhwala Tidziwane maudindo wawa Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ndili ndi maudindo angapo, ndine nduna ya mfumu mdera lino. Ndimamemeza anthu ammudzi muno ngati pali zina kuti zichitike kapena mfumu yaitana. Ngati anthu ammudzi muno ali ndi zochita zina monga mwa zikhulupiriro zawo amandifikira kuti ndipereke uthenga kwa mfumu yathu yomwe imaloleza zochitikazo komanso kudambwe ndili ndi gawo langa. +Tikambe nkhani ya gulewamkulu Mufuna ndikambe nkhani iti kumeneku? Pajatu zakudabwe saulula, mumadziwa zimenezo? Inde koma, nzabwinobwino, osati zofwala gule. +Chabwino, nkhani yake ndi yotani yomwe mufuna ticheze? Tikumva kuti guleyu ndi mankhwala, ndi zoona? Ndi zoona. Ife Achewa timakhulupirira zimenezi. Izi kuno zimachitika ngati mizimu yalamula kuti tichite. +Zimakhala bwanji kuti mpaka zifike poitana gule? Timakhala talamulidwa ndi mizimu kuti gulewamkulu avine ndi cholinga chochotsa matendawa. Izi sizitheka popanda kulamulidwa ndi mizimu. +Talongosolani chiyambi chake chimakhala chotani kuti mizimu ilamule? Munthu ngati akudwala, timayenda naye mwa asinganga momwe timakaombeza za chiyambi cha matendawo. Kumeneko nkomwe amanena ngati matendawo akufunika kuvinira gule kapena angomwa mankhwala. Apa ndikutanthauza kuti sizingatheke kuti mungoyamba kuvinira matenda ngati mizimu sidanene. +Akati gule akavine zimakhala bwanji? Amanena kuti mukatenge chikho cha msunje ndipo tikaikemo ufa ndi kukanda. Apa mumayamba kumuzungulitsa chikho chija. Pomwe mukuzunguliza chikho chija mumaimba nyimbo. Tikatha amati tikataye patsinde pa mtengo. Pomwe tikuchita izi ngoma zimakhala zikusweka komanso zilombo zikuvina. +Taimbani nyimboyo ndimve Timati.Tidzutsire wathuyu bwino, ngati ndi mizimu wathuyu adzuke. Mizimu mudzutse wathu pofika mawa Kodi matendawa amakhala atafika pothiphwa kwambiri? Eee! Matenda amakhala afika povuta ndipo tikamati tidzutsire wathuyu ndiye kuti amakhala salinso mwakanthu. +Akamati mukavine gulewamkuluyo amakupatsani mankhwala alionse? Palibe mankhwala alionse omwe amatipatsa ndipo machiritso amagona pamenepo. Mukavina ndi kutsata zomwe akunenazo matenda amathera pomwepo. +Ndani amayenera kupezeka pamwambo ngati umenewo? Akuluakulu a gule amapezeka pamalopo komanso mwini mbumbayo. Pomwe tikusankha mwini mbumba timayenera kusankha yemwe adalowa gule wamkulu osangotenga aliyense. +Kodi zimatheka kuti gule avine chikhalirecho sindiwe wolowa? Sizingatheke. Kuno zimachitika chifukwa aliyense adameta kapena kuti kugula njira. +Akana nyau yogwiririra Senior Chief Lukwa, mmodzi mwa mafumu akuluakulu a Achewa mdziko muno, yemwenso amayankha pankhani za mafumu, wati munthu yemwe khothi mboma la Dedza lidamupeza wolakwa pamlandu wogwiririra si wagulewamkulu monga momwe iye adakonzera kuti zioneke. +Khothi la Dedza, lomwe wogamula wake adali First Grade Magistrate Enett Banda, lidapeza Lazaro Maxwell, wa Zaka 19, wolakwa pamlandu wogwiririra mtsikana wa zaka 14 atadzizimbaitsa ngati gulewamkulu kuti asadziwike ndipo lidagamula kuti akagwire ndende yakalavulagaga kwa zaka 8. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Achewa amalemekeza gulewamkulu chifukwa ndi gule wa mizimu Malingana ndi apolisi mbomali, Maxwell adavomera mlanduwo mbwalolo ndipo woimira boma pamlanduwo, Inspector Wedson Nyondo, adapempha bwalololo kuti lipereke chilango chokhwima kwa wopalamulayo kaamba koti woyimbidwa mlanduyo adanyozetsa chikhalidwe cha Achewa. +Mpofunika kulingalira kuti munthuyu wanyazitsa chikhalidwe cha Achewa chomwe eni ake amateteza kuyambira kalekale kotero, nkofunika kumpatsa chilango chokhwima kuti zotere zisamachitikechiteke, adatero Nyondo. +Poperekapo maganizo ake pankhaniyi, Senior Chief Lukwa adati munthu yemwe adachita izi si wagulewamkulu yemwe amadziwika kuti ndi gule wa mizimu, koma munthu wazifukwa za mtopola wofuna kunyazitsa Achewa. +Lukwa: Umenewo ndi mtopola Uwu ndiye timati mtopola. Mdziko muli khalidwe lolemekezana ndi kulemekezerana miyambo ndi zikhulupiriro zoyenera ndipo Mchewa weniweni sangachite zimenezi. Ameneyu ndi munthu wongofuna kuononga mbiri yabwino ya Achewa, adatero Lukwa. +Iye adati khothi lomwe lidagamula mlanduwo lidachita bwino kumulanga chotero kuti iye ndi ena anzeru zangati zakezo atengerepo phunziro lolemekeza mitundu ndi miyambo a anthu. +Malingana ndi umboni umene udaperekedwa mbwalo la milandulo, pa 8 mwezi womwe uno, Maxwell ndi mnzake wina yemwe sadatchulidwe adadziveka ngati gulewamkulu pomwe adakumana ndi msungwana wogwiririridwayo patchire lina lomwe limalekanitsa midzi ya Bowazulu ndi Kalipande. +Umboniwo udapitirira kenena kuti msungwanayo atangodutsana ndi gulewamkuluyo, Maxwell adayamba kumuthamangitsa ndipo atamugwira adamukokera patchire nkumugwiririra. +Poti wogwiririrayo adali mchigoba, msungwanayo adati munthu woyambirira kumuganizira adali Maxwell chifukwa adakhala akumuvutitsa kuti amamufuna chibwenzi koma amamukana ndipo nkhaniyi itafika kukhothi iye sadataye nthawi koma kuvomera mlanduwo. +Mlandu wogwiririra mwana wamngono umatsutsana ndi ndime 138 ya malamulo ogamulira milandu ndipo munthu akapezeka wolakwa, chilango chake chachikulu ndi zaka 14 akugwira ntchito yakalavula gaga kundende. +Maxwell amachokera mmudzi mwa Chatondeza pomwe msungwanayo amachokera mmudzi mwa Kalipande kwa T/A Chilikumwendo mboma la Dedza. +Mpendadzuwa ungatukule malawi Mkulu wa bungwe la Farmers Union of Malawi (FUM) Alfred Kapichira Banda, wati pakuyenera kukhala ndondomeko yabwino pakati pa alimi, misika, komanso boma kuti mpendadzuwa uzilimidwa ochuluka. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Polankhula ndi Uchikumbe, iye adati makampani komanso makopaletivi omwe amagwiritsa ntchito mpendadzuwa popanga mafuta ophikira atagwirizana ndi alimi komanso boma, mpendadzuwa ukhonza kumalimidwa mochuluka zomwe zingapangitse kuti mafutanso azipangidwa ochuluka. +Phindu la mpendadzuwa ndi losayamba Mafutawa akhonza kumagulitsidwa mMalawi momwemuno ngakhalenso kunja, adatero mkuluyo. +Izi zikugwirizana ndi zomwe adanena Cliff Chiunda, mlembi wamkulu muunduna wa za migodi, malonda ndi zokopa alendo mmbuyomu kuti dziko la Malawi lingapulumutse K3 biliyoni zomwe limaononga pogula mafuta ophikira kunja chaka chilichonse. +Kapichira Banda adati: Ambiri akuthamangira kulima fodya chifukwa msika wake siuvuta. Pomwe fodya akulimidwa wochuluka, mitengo imatsika ndipo wina amabwerera. Ena akadamalima mpendadzuwa bwenzi akusimba lokoma, adatero iye. +Iye adati boma limayenera kulimbikitsa alimi pa za mbewuyi ndipo mpendadzuwa ukupambana fodya chifukwa amapangira mafuta ophikira omwe pafupifupi aliyense amagwiritsa ntchito pomwe si onse amasuta fodya. Mkuluyo adaonjezanso kuti mpendadzuwa sulila feteleza ngati mbewu zina komanso mmunda mwa mbewuyi simumera udzu kwambiri. +Mathias Banda, wapampando wa kopaletivi ya Talimbika Agro-Processing and Marketing yopanga mafuta ophikira otchedwa Sunpower kuchokera ku mpendadzuwa mboma la Salima, adati anthu sakukhala ndi chidwi ndi ulimiwu. +Tili ndi alimi athu omwe timawalangiza momwe angalimire mpendadzuwa ndipo pamapeto pake amatigulitsa koma sukwanira kupangira mafuta chaka chonse kotero timayendayenda kusakasaka komwe tingaupeze. Tangoganizani, timachoka ku Salima kukagula ku Phalombe ndipo kumeneko ukatha timalowa mdziko la Mozambique konseku kuli kusaka mpendadzuwa, adatero Banda. +Iye adaonjeza kuti izi zimapangitsa kuti azipanga mafuta ochuluka mnthawi yokolola yokha ndipo ikangodutsa amapanga mafuta ochepa. Iye adafotokozanso kuti mafuta awo ndi ovomerezeka ndi a Malawi Bureau of Standards (MBS) ndipo yapeza kale misika mmaiko a kunja koma nkhawa yawo ndiyoti azikapeza kuti mpendazuwa ochuluka. +Mpendadzuwa suvuta kulima ndipo umacha pakutha masiku 60. Mlimi amangodikira masiku 10 owonjezera kuti ayambe kukolola. Pa ekala imodzi yokha mlimi akhonza kukolola makilogalamu 2000 akausamalira bwino, adatero Banda. +Iye adaonjezanso kuti alimiwa akuyenera kulima mpendadzuwa pomwe mvula ikugwa yochuluka kuti awuteteze ku anunkhadala. +Anunkhadala amaononga mpendadzuwa ukangomera kumene makamaka ngati mvula siikugwa yokwanira kotero mlimi akhonza kubzala kangapo. Akabzalidwa pamene mvulayi ikugwa yochuluka, anunkhadala amasokonezeka, adatero iye. +Banda adati mbewuyi imachita bwino paliponse koma imachita bwino kwambiri mmadambo. Iye adati mizere yake imayenera kutalikirana ndi masentimita 75 ndipo pobzala, utalikirane ndi masentimita 25 ngati ukubzalidwa umodziumodzi ndipo utalikirane, masentimita 45 kulekezera 60 ngati ukubzalidwa uwiriuwiri. +Maule akusambabe wamkaka Khomo la ukwati silisowa. Mbanja la Nyasa Big Bullets kudakali chisangalalo kutsatira chipambano chawo pobabata asilikali a ku Mzuzu, Moyale Barracks. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Inde ndi asilikali, koma Loweruka lapitali adalira ndi kukukuta mano atadzidzimutsidwa ndi Bullets yomwe idachita ukali kumapeto kwa masewerowo pamene Moyale imafuna iyambe kusangalala. +Ichotu chidali chikho cha Presidential Cup chomwe wopambana adatenga K10 miliyoni ndipo wogonja kutenga K5 miliyoni. +Moyale idachinya pa mphindi 38 mchigawo choyamba kudzera mwa Wiseman Kamanga. Idalimba poteteza chigolicho mpaka mphindi 90 mchigawo chomaliza. +Ochemerera Bullets kusamba mkaka Goloboyi wa Moyale, Juma Chikwenga ndi osewera onse a Moyale adayamba kupha nthawi apo woimbira Duncan Lengani akuganiza zothetsa masewerowo ikangotha nthawi yoonjezera. +Mpanipani udali ku Bullets ndipo mphunzitsi wawo Franco Ndawa adalowetsa osewera kutsogolo anayi; Chiukepo Msowoya, Diverson Mlozi, Mussa Manyenje ndi Aimable Nikiyiza ndipo Bullets imadza ngati mbandakucha. +Patatha mphindi 93, wosewera wa Moyale adachita thengenenge mpaka kugwira mpira kupezetsa Bullets penote ndipo Msowoya adachinya kuti masewerowo alowe mmapenote. +Pilirani Zonda ndi Msowoya adaphonya mapenote a Bullets pamene Yamikani Fodya, Miracle Gabeya, Nikiyiza ndi Fisher Kondowe adachinya. +Love Jere ndi Chrispine Fukizi a Moyale adagwiritsa mapenote awo ndipo Sandress Munthali, Mtopijo Njewa ndi Timothy Nyirenda adamwetsa. Boy Boy Chima adamenyetsa chitsulo kupangitsa kuti Maule atenge chikhochi. +Ochemerera Bullets adayenda ndi mimba, ena kuvula zovala ndi ena kusamba mkaka kusangalala kuti timu yawo yatenga chikho. Osewera a Moyale adagwa pansi, kulira mosatonthozeka. +Fodya adati loto tsopano lasanduza zochitika, Mulungu adali mbali yathu, zidali zovuta koma Mulungu wazitheketsa, adatero iye. +Alipa nkhuku 70 atatayira chimbudzi pachitsime Gulupu Chinyamula kwa T/A Kamenyagwaza mboma la Dedza walipitsa amayi awiri nkhuku 35 aliyense chifukwa chotaira chimbudzi pachitsime. +Iye walamulanso kuti nyakwawa Chinyamula alipe nkhuku ziwiri chifukwa milanduyi idagwa mmudzi mwake. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Gulupu Chinyamula adati sabata yatha, mjigo wa mmudzi mwawo udaonongeka ndipo akulephera kukonza. +Malinga ndi gulupuyu, anthu 1 500 a mmidzi 10 imene ili pansi pake amamwa mjigo umodzi ngakhale akhala akudandaula kwa a mabungwe kuti awakumbire wina. Kaamba ka kuchuluka kwa anthu ogwiritsira ntchito mjigowu, sikuchedwa kuonongeka. +Aka sikoyamba kuti mjigo uonongeke, wakhala ukuonongeka kuyambira chaka chatha. Pamene waonongeka, midzi yonse imakamwa pachitsime pamene achitira chipongwepo. +Tsono ulendo uno, pamene anthu anapita kukatunga pachitsimecho, adadabwa kuti munthu wachitiramo chimbudzi. Koma amene adapita mmawa, ataona zofiira mmadzimo, amangoti ndi masamba ndipo adatunga ndi kukagwiritsira ntchito madziwo, adatero gulupuyu. +Iye adati anthu amene adabwera pachitsimepo dzuwa litatuluka ndiwo adazindikira kuti pachitsimepo wina wachitira chimbudzi. +Nyakwawa Chinyamula adati anthuwo adamuitanitsa kuchitsimeko ndipo idadzionera yokha kuti idali ndowe ya munthu. Kodi adaidziwa bwanji? Ine ndisadziwe chimbudzi cha munthu? Amene adatungawo adandionetsa ndipo ndidatsimikiza chifukwa pa nthawiyo nkuti isadasungunuke, idatero nyakwawayo. +Nkhaniyo itapita kwa gulupu Chinyamula, iye akuti adaopseza kuti ayenda ndi chimbudzicho kwa nganga kuti amene wachitayo aone mbonaona. +Tsiku lomwelo padabwera amayi awiri amene adati ndiwo adachita zimenezo. Sadafotokoze bwino chifukwa chomwe achitira izi koma adavomera pamaso panga kuti adakataya chimbudzicho ndiwo, adatero gulupuyu. +Gulupu Chinyamula wati amaiwo adauza bwalo lake kuti adachita chipongwecho ngati njira imodzi yoti akuluakuku akonze mjigowo mwachangu. +Nkhaniyi itapita kubwalo, gulupuyo adagamula kuti mayi aliyense alipe nkhuku 35. Mayi mmodzi wapereka kale nkhukuzo pamene wina wangopereka nkhuku 15. +Ndalandira nkhuku 35 kwa mayi mmodzi komanso nkhuku 15 ndipo kwatsala nkhuku 20, adatero gulupuyu. +Iye wati bwalo lake limaloledwa kulipitsa nkhuku. Ndine gulupu, nkhani ikafika pabwalo langa, ndimalipitsa nkhuku basi. Bwalo la T/A limalipitsa mbuzi pamene kubwalo la paramount kumagwa ngombe, adatero pamene olakwawo sadapatsidwe mwayi wolipira ndalama akalephera kulipa nkhuku. +Nkhukuzi tigulitsa ndipo ndalama yake tikonzetsera mjigowu, mafumu anga ndawauza kale za nkhaniyi ndipo ntchito yokonza mjigowu iyamba sabata ikudzayi, adatero. +Nyakwawa Chinyamula wati anthu asiya kugwiritsira chitsimecho ndipo akumba zitsime zina kumadimba komwe akulima mizimbe. +Tidaitanitsa wa zaumoyo kuti adzathire mankhwala pachitsimepo koma mpaka pano sadabwere, chomwe tapanga ndikukumbanso zitsime zina kumadimba komwe tikumwa pano, idatero nyakwawayi. +Akhazikitsa tindege tothandiza zaumoyo Pali chiyembekezo chakuti mavuto omwe amakumana nawo ogwira ntchito mzipatala za kumidzi ndi anthu okhala mmaderawo achepa ndi makina a tindege otchedwa drone mChingerezi polumikizitsa maderawa ndi zipatala zikuluzikulu. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Unduna wa Zaumoyo, nthambi yoyendetsa za maulendo a pa ndenge ndi bungwe loyanganira za umoyo wa ana la Unicef atsimikiza za ndondomekoyi yomwe ati yayamba kale kugwira ntchito mmadera ena. +Kamodzi mwa tindegeto Mneneri wa bungwe la Unicef Doreen Matonga wati ogwira ntchito mzipatala za kumidzi amakumana ndi mavuto adzaoneni popereka ndi kulandira thandizo la zaumoyo komanso pakakhala ngozi zodza mwadzidzidzi Madera ena amavuta kufikako. +Iye adati mavuto odziwika kwambiri ndi nkhani ya mayendedwe pokatenga mankhwala kuchipatala chachikulu kapena pokayezetsa magazi ndi makhololo komanso polandira zotsatira za zoyesazo. +Tidapeza kuti pali zipatala zina zomwe ogwira ntchito amayenera kupalasa njinga mtunda pafupifupi makilomita 70 kuti akatenge mankhwala kuchipatala chapaboma ndi kubwereranso mtunda onga omwewo. +Kuwonjezera apo, pakakhala zofunika kuyeza monga malungo kapena makhololo, pamatenga nthawi kuti zikafike ku chipatala chomwe amayeza komanso kuti zotsatira zake zifike pomwe wodwalayo akungodikilira, adatero Matonga. +Iye wati apa azikgwiritsa ntchito tindegeto, timenenso tizithandiza kujambula zithunzi za Madera amene kwagwa ngozi komanso kupititsa patsogolo ntchito za Internet. +Mneneri wa unduna wa zaumoyo Adrian Chikumbe wati ndondomekoyi idayamba mmwezi wa February mmadera ochepa ndipo idakhazikitsidwa mwezi watha kuti iwunikidwe ngati ndiyothandizadi. +Ikangogwira, mavuto ambiri atha chifukwa nzoonadi kuti anthu a mmadera a kumidzi amakumana ndi mavuto kuti alandire thandizo moyenera, adatero Chikumbe. +Woyanganira za maulendo a ndenge ku unduna wa za mtengatenga Hastings Jailosi wati ndondomeko yonse yaunikidwa kale bwinobwino ndipo sipazikhala kusokonezana pakati pa tindengeti ndi ndenge zikuluzikulu zonyamula anthu ndi katundu. +Iye wati tindegeti tikhala mmasayizi osiyanasiyana ndipo tizinyamula katundu wa milingo yosiyanasiyana. +Tina tikhoza kunyamula katundu wolemera makilogalamu 25 ndipo tina ntocheperako, adatero Jailosi. +La Nina wachita katondo Mmene mitambo ya mvula imachita mikhwithi ndipo mvula idayamba kugunda, gogo Justina Nya Chilembo, wa zaka 65, adali ndi chisangalalo komanso chiyembekezo kuti chaka chino abzala msanga. +Gogoyu, wa mmudzi mwa Chibo, kwa Paramount Chief Chikulamayembe mboma la Rumphi, sadayembekezere kuti akhala mmodzi mwa anthu oyambirira kumva ululu wa nyengo ya La Nina, imene mvula imagwa mosakaza. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Nyumba yake ya zipinda zitatu momwe amakhala ndi ana aamuna awiri kuphatikizapo wamkazi ndi zidzukulu zingapo, idasasuka denga lofolera ndi malata, kaamba ka chimvula chomwe chidabwera ndi chimphepo chamkuntho sabata ziwiri zapitazo mderalo. +Chifukwa sadakonzekere za ngozi yotere, gogo Nya Chilembo, yemwe ndi wamasiye, pano akusowa mtengo wogwira chifukwa katundu wambiri mnyumbamo, kuphatikizapo chakudya, adaonongeka. +Sindikudziwa kuti nditani nawo anawa ndi zidzukuluzi tsopanoSindikudziwa komwe ndingapeze ndalama zoti nkufoleranso nyumbayi, kaya nditani ine wamasiye! adalira choncho, poyankhula ndi Tamvani msabatayi. +Nya Chilembo: Sindikudziwa nditani Anthu ambiri mderali ndi madera ena mdziko muno adakhudzidwa chimodzimodzi ndipo akusowa mtengo wogwira chifukwa mvulayo idawadzidzimutsa ndi magwedwe ake osakaza. +Inde, yafikanso nyengo yolira pamene madzi osefukira ndi mvula yodza ndi mphepo yamkuntho zasamutsa kale anthu komanso kugwetsa nyumba mmaboma 13 mdziko muno. +Naye Chimwemwe Bonifasiyo wa mmudzi mwa Chikaola kwa T/A Kachindamoto ku Dedza adati nyumba yake idasasuka ndi mvula ya mkuntho yomwe idagwa kumeneko. +Ndidathawa pakhomo ndipo ndidabwera mvula itatha. Katundu adanyowa komanso nyumba idasasuka, adatero. +Ndipo Felina Kuyaka wa mmudzi mwa Pemba kwa Senior Chief Kawinga mboma la Machinga wati pano akugona mkitchini kutsatira kugwa kwa nyumba yake. +Kuyaka akuti ana ake atatu adavulala ndi mvulayo. +Nyumba idagwa, ana avulala ndipo ali kuchipatala. Katundu adaonongeka, adatero Kuyaka. +Mneneri wa nthambi ya boma yoona ngozi zogwa mwadzidzidzi ya Department of Disaster Management Affairs (Dodma), Jeremiah Mphande watsimikiza kuti padakalipano, vutoli lakhudza maboma a Balaka, Machinga, Mangochi, Nsanje, Dedza, Dowa, Karonga, Rumphi Mzuzu, Chiradzulu, Phalombe, Zomba ndi Nkhotakota. +Iye adachenjeza anthu amene akukhala malo angozi monga odikha kuti asamuke, ndipo adaonjeza kuti nthambiyo yakonzeka kuthana ndi mavutowa. +Tidadziwitsidwa mmbuyomu ndi anzathu amene amalosera momwe nyengo ikhalire amene adatiuza kuti tikhala ndi mvula yambiri chifukwa cha nyengo ya La Nina. +Pachifukwachi, tidafika mmaboma onse ndipo tidaikamo gulu lomwe lizitipatsa malipoti zikangochitika komanso thandizo lomwe likufunika, adatero Mphande. +Ngakhale nthambiyo yakonzeka, Mphande adati kupewa kuposa kuchiza kotero anthu amene akukhala malo angozi asamukiretu zinthu zisadafike poipa kwambiri. +Okhala madera amene madzi atha kufika, ayenera kusamukira kumtunda chifukwa chaka chino tilandira mvula yambiri. Iyi ndi njira yokhayo yopewera mavutowa, adatero Mphande. +Iye adati chaka chino chingathe kuposa chaka chatha chifukwa mvula yangogwa sabata zochepa koma madera amene samachitikachitika ngozi akhudzidwa. +Ndi chisonyezo kuti zinthu ziipa chaka chino. Nchifukwa tikuti anthuwa asamukire kumtunda, adaonjeza. +Nthambi yoona za kusintha kwa nyengo ya Department of Climate Change Management and Meteorological Services idalosera kuti chaka chino kukhala nyengo ya La Nina yomwe ingapangitse kuti kukhale napolo. +Malinga ndi nthambiyo, La Nina amapangitsa kuti mvula ibwere yochuluka ndipo zigawo zakummwera ndi kumpoto kwa dziko lino ndi komwe adati kugwa mvula yoposera mlingo wake. Zamveka kuti munthu mmodzi wafa pangozi ya mvula. +Mboma la Balaka, mvula ya mkuntho yasokoneza midzi ya mwa T/A Chanthunya ndipo nyumba 278 zasasuka. Sukulu komanso nyumba zopemphereramo zagwa ndipo anthu anayi avulala. +Malinga ndi lipoti la ofesi ya DC, mvula ya mkuntho ndiyomwe idavuta kumeneko ndipo anthu akusowa pokhala komanso minda yawo yakokoloka. +Ku Karonga, mvula ya idasakaza ndi kugwetsa nyumba 106 kuyambira pa November 30 mpaka December 2 mmadera a T/A Wasambo ndi Senior Chief Kyungu. +Lipoti la DC lati anthuwa akusowa pokhala komanso akusowa chakudya ndipo akufunika thandizo lachangu. +Ku Machinga nyumba 395 zasasuka komanso nyumba zopempherera ndi sukulu zasasuka. +Wothandizira mkulu woona za ngozi zogwa mwa dzidzidzi mbomalo, Shephard Jere, adati nyumbazi ndi za mwa T/A Chikweo, Kawinga ndi Nkoola. +Ku Mangochi, ngozi ya mvula yamphepo idachitika pa 5 December ndipo nyumba 587 zidagwa malinga ndi lipoti la wothandizira mkulu woyanganira ngozi zogwa mwadzidzidzi Carlo Chabwera Millinyu. +Ku Dedza, nyumba 196 zagwa chifukwa cha mvula ya mphepo ndipo mayi mmodzi adamwalira komanso ena kuvulala. Izi zidachitika mdera la T/A Kachindamoto komanso Chilikumwendo. +Malinga ndi lipoti la DC wa bomalo James Kanyangalazi, mabanja okhudzidwawa akufunika thandizo lachangu zomwe ndi malo okhala komanso chakudya. +Ku Dowa, nambala ya mabanja amene akhudzidwa sadadziwike koma ma T/A atatu ndiwo akhudzidwa monga Chakhaza, Chiwere ndi Msakambewa. +Akukambirana zolola ana a chi Rasta msukulu Unduna wa za maphunziro wati ukukambirana ndi ma Rasta komanso unduna wa za malamulo pa za ana 26 amene ma Rasta adapempha kuti aziloledwa kuphunzira msukulu za boma ali ndi tsitsi la mizeremadiredi. +Anawa, amene padakali pano sakupita kusukulu, akuimira ana ena onse a ma Rasta amene amaletsedwa kusunga tsitsi lopotana msukulu za boma za mdziko muno. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mwanamanga: Tinkakambirana ndi Bingu Kalata yomwe unduna wa za malamulo udalembera unduna wa za maphunziro pa 27 January, 2017, idaunikira kuti undunawo ukuyenera kulandira mwana aliyense, kuphatikizapo ana amene akusunga tsitsi lopotana, malinga ndi chipembedzo chawo. +Potengera ndi kulemekeza mphamvu ya malamulo a dziko lino, pa magawo 20, 25 ndi 33, ndi ufulu wa mMalawi, aliyense kusasalidwa ndipo munthu aliyense ali ndi ufulu wolandira maphunziro komanso otsatira chipembedzo chomwe akufuna. +Kotero, potengera kusintha lamulo lokhudza maonekedwe ndi za kavalidwe pakati pa ophunzira, lomwe limaletsa kusunga tsitsi pasukulu, mukuyenera kulola ana omwe ali ndi tsitsi lopotana potengera chipembedzo cha chi Rasta msukulu za boma, idatero kalatayo. +Mneneri wa unduna wa za maphunziro Lindiwe Chide adati undunawu ukudziwa za kalata yochokera ku unduna wa za malamuloyo ndipo adati undunawo ukukambirana ndi mbali zonse zokhudzidwa pa momwe izi zingatsatidwire. +Tikukambirana ndi mbali zosiyanasiyana zokhudzidwa za momwe tingayendetsere pulogalamuyi ndipo zikatheka mumva sizidzasowa, adatero Chide. +Sukulu za boma za pulaimale ndi sekondale mdziko muno zimathamangitsa ana omwe ali ndi tsitsi lopotana potsatira chipembedzo cha u Rasta ndipo nkhaniyi siyikondweretsa mpangono pomwe eni chipembedzochi. +Kwa zaka zoposa 20 tsopano, otsatira chipembedzochi akhala akumenyerera kuti unduna wa zamaphunziro usinthe maganizo nkuyamba kulola anawa msukuluzi kuti nawonso azidyerera ufulu wawo wamaphunziro. +Mtsogoleri wachipembedzochi mdziko muno mgawo la Nyabinghi, Ras Mikah Chiserah wati zomwe zikuchitikazi zikutanthauza kuti dziko la Malawi silivomereza chipembedzo cha chi Rasta monga momwe malamulo amanenera. +Apatu zikutanthauza kuti ife ma Rasta tikufera chipembedzo chonsecho malamulo amati munthu aliyense ali ndi ufulu otsata chipembedzo chomwe akufuna pambali pa ufulu wa maphunziro, adatero Ras Chiserah. +Iye adati pomwe ufulu wa zipembedzo unkabwera kumayambiliro a ulamuliro wa zipani zambiri, iwo ankaona ngati kuponderezedwa kwa owutsatira kwatha koma akudabwa kuti boma likulephera kutsatira malamulo opanga lokha. +Kadaulo pa zamalamulo yemwenso ndi mphunzitsi ku sukulu ya ukachenjede ya Chancellor College ku thambi ya zamalamulo, Edge Kanyongolo adati ufulu uli ndi mlingo wake koma akaunika nkhani ya ma Rastayi, saonapo vuto. +Mmalamulo a dziko lino muli maufulu osiyanasiyana ndipo umodzi mwa maufuluwa nkukondedwa mofanana. Chifukwa chokhacho chomwe ufulu ungapatsidwe mlingo, mpomwe ukuphwanya ufulu wa anthu ena ndipo sindikuona kukhala ndi tsitsi lopotana kukuphwanya ufulu wa munthu wina, adatero Kanyongolo. +Malingana ndi mneneri wa Nyabinghi, Ras Fred Mwanamanga, kusunga tsitsi lopotana ndi umodzi mwa mizati ya chipembedzo cha chi Rasta ndipo kuti ngati Amalawi, otsatira chipembedzochi amayenera kuloledwa kupanga chilichonse chomwe otsatira zipembedzo zina amaloledwa kupanga. +Pomenyerera ufulu wa maphunziro omwe Mwanamanga adati otsatira chipembedzochi amamanidwa, ma Rasta adakumana ndi mtsogoleri wakale Bingu wa Mutharika yemwe adawalonjeza kuti zonse zikhala bwino. +Mwanamanga adati mwatsoka, zisadakhale bwino monga momwe amayembekezeramo, Mutharika adamwalira ndipo izi zidachititsa kuti ma Rastawa ayambirenso nkhondo yomenyerera ufulu wawo. +Titangomva za imfa ya a Mutharika, tidasweka mitima chifukwa tidadziwa kuti ntchito ikadalipo. Mu 2013, tidayenda ndawala yokapereka kalata ya madandaulo kulikulu la dziko lino ku Lilongwe komwe tidayankhidwa kuti madandaulo athu apita kwa a Pulezidenti, watero Mwanamanga. +Iye wati pakhala pakuchitika zokambirana pankhaniyi pakati pa ma Rasta, unduna wa zamaphunziro, unduna wa za malamulo ndi magulu a zamaufulu ndipo potsatira zokambiranazi, unduna wa za malamulo udalangiza unduna wa za maphunziro kuti uyambe kupereka mpata kwa ophunzira a chipembedzo cha chi Rasta. +Malonda a chamba avuta ku Nkhata Bay Zikuoneka kuti chamba (ena amati kanundu) ndi malonda otentha mboma la Nkhata Bay. Chaka chatha chokha anthu 25 adapezeka ndi milandu yokhudza katunduyu moti ngakhale chaka chino sichinathe, milandu 17 yokhudza chamba yapalamulidwapo kale. +Mlandu wauwisi ndi wa mayi wa zaka 34, Angela Banda, yemwe adapezeka ndi zikwama ziwiri zikuluzikulu zodzadza ndi chamba pa Roadblock ya Mukwiya mbomali. Banda adakwera basi pa Dwanga ulendo wa ku Mzuzu sabata yathayi. Mwatsoka, ulendowu udathera mmanja mwa apolisi. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Katundu wovuta: Apolisi atagwira galimoto yonyamula shuga ndi matumba a chamba Banda amachokera mmudzi mwa Msomba kwa mfumu yaikulu Mabuka mboma la Mulanje. +Malinga ndi mneneri wa polisi mbomali, Ignatious Esau, anthu a zaka zosapitirira 30 ndiwo akupalamula kwambiri. +Esau adati malondawa akhoza kukhala otentha chomwechi mbomali chifukwa ndi limodzi mwa maboma omwe amakopa kwambiri alendo kaamba ka nyanja. +Komanso tikuona ngati chifukwa bomali lili mmalire a dziko lino ndi la Mozambique, choncho izi zitha kukhala zothandizira popititsa patsogolo malonda oletsedwawa, adatero Esau. +Iye adati ngangale zili chomwechi, apolisi akuona kusintha. +Malinga ndi Esau, chiwerengerochi chatsikako pangono kaamba koti nawo mabwalo a milandu alowererapo tsopano. +Mabwalo athu akuperekano chigamulo chokhwima kwa onse opezeka ndi mlandu wokhudza chamba, adatero Esau. +Iye adati zafika poti apolisiwa akumayendanso msukulu kuphunzitsa ana za kuipa kosuta kanundu. +Malamulo a dziko lino, salola kubzala, kugulitsa kapena kusuta chamba ndipo aliyense wogwidwa akuchita izi amazengedwa mlandu mogwirizana ndi gawo 4a lowerengedwa limodzi ndi Lamulo 19 (ndime 1 ndi 2) la mankhwala oopsa. +Mudali mgalimoto ulendo ku Area 23 Kumwetulira kwa Shreen Mbendera, muulutsi pawailesi ya Galaxy FM, kunachititsa kuti Kimu Kamau amuthere mawu namwaliyu. Ukwati walengezedwa kale kuti ndi pa 29 October chaka chino. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kamau, yemwe akugwira ku Union Building Contractors ngati woyanganira chigawo chapakati, lero alibenso mawu. October akumuona kuchedwa malinga ndi momwe June waziziriramu. +Kamau akuti idali ntchito yaikulu chifukwa mtsikanayu amalimba chifu kuti pavute patani, Kamau yekha ayi. Mapemphero adathandiza ndipo tsiku lidakwana kuti Shreen akhale ndi mawu omaliza pa Kamau. +Akuti mudali mu 2014 pomwe adamutenga Shreen ulendo naye ku 23 komwe namwaliyu amakhala komwenso ndikoyandikana ndi kunyumba kwa Kamau. +Akuti akamwetulira Shreen Kamau mawu onse balala Pumbwa wakankhidwira kuchipwete! Apa nkuti nditamudziwa kale Shreen chifukwa tidakumana ku Galaxy pamene ndidapita kukaona mnzanga. Pokaona mnzangayo, mpamene pamabwera Shreen yemwe amacheza ndi mnzangayo. +Inenso ndidayamba kumacheza ndi namwaliyu mpaka pamene ndidayamba kumufuna nditazindikiranso kuti sadali pabanja, adatero. +Komabe Kamau akuti sakadatha kukhala nthawi yaitali asadathire mawu namwaliyu chifukwa cha zomwe zimatakasa mtima wake. +Akati amwetulire, komanso maonekedwe ake, eeh ndidafuna ndichite kanthu kuti zimenezi ndizikazionera pafupi, adayamikira Kamau. +Adayesera kutulutsa mawu osiyanasiyana koma namwaliyu adakana. Ndidayendera mpaka kutopa, kuyesera kukamba za manifesto yanga yonse koma osavomera. Kenaka ndidadabwa akundiyankha mmenemo nditataya chikhulupiriro, adatero Kamau. +Nthawi ya Mulungu ndiyo nthawi yabwino, chilichonse chili ndi nthawi yake. Amene akusaka, afunse kaye Ambuye ndipo adzawapatsa wachikondi weniweni, adatero namwaliyu. +Ukwati wawo ukachitikira ku Banja Loyera Parish ku Chilinde 2 mumzinda wa Lilongwe. Shreen ndi wa mmudzi mwa Gambatula kwa T/A Chakhumbira mboma la Ntcheu ndipo Kamau ndi wa mmudzi mwa Mpagaja, kwa Senior Chief Somba ku Blantyre. +Tisiyanitse kukongola ndi kuphweka Amayi ndi atsikana ambiri tikafunsiridwa ndi munthu wokwatira, timakwera mumtengo, kumva bwino kuti ngakhale uja ali ndi mkazi wake waponyabe maso pa ine ndiye kuti ine ndiliko bwino poyerekeza ndi mkazi wake. +Enanso omwe amachita zibwenzi ndi abambo okwatira maganizidwe ake amakhalanso otere: Umaona ngati kuti iwe wachibwenziwe ndiwe swopambanirako kusiyana ndi mkazi ali kunyumba. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mayi wanga adandiuza, ndipo ndimakhulupilirabe mpaka lero, kuti kufunsiridwa ndi munthu wokwatira si chinthu chopambana koma chomvetsa chisoni. +Iwo adati bambo wa banja lake akati wakukonda, udzidabwe ndipo udandaule kuti waona chiyani pa iwe. +Ndi nkhani ina kuti wakunamiza kuti ngosakwatira, koma ukudziwa ndithu kuti ali ndi mkazi kunyumba, iye nkulimba mtima nkubwera kwa iwe ndi mawu achikondi ndiye kuti wakudelera; wakuona kuphweka. +Ambiri mwa abambowa amakukweza mumtengo pokuuza zabwino zako poyerekeza ndi mkazi wawo. Iwe ukakhala watulo umangogodoka. +Ena amakuuza za mavuto omwe akukumana nawo kunyumba, iwe nkumadziona ngati msamaliya woti uthandize kukonza moyo wa bambo yemwe sakusangala kunyumba kwake. +Koma zoona zake nzakuti abambo ambiriwa amangofuna kukuseweretsa. Amangofuna akupusitse ndiye iwe ukakhala opepera ndi wotengeka ndi timau tabodza tachikondi umagwa mmbuna. +Ena mwa abambowa amakuuza kuti ali ndi maganizo othetsa banja lawo. Iwe nkumalimba mtima uli ndikalowa ndine mnyumbamo mzangayo akathamangitsidwa. +Umangodabwa zaka zikupita ana nkumabadwa mnyumba muja bamboyo akuti sakukondwamo. Ndipo kawirikawiri likatha banjalo abambo oti amachita chibwenzi ndi iwe samakukwatiranso. Amakasaka wina mzimayi wakhalidwe iwe nkungokugwiritsa fuwa la moto. +Nkutheka mwina wakukondadi bamboyo, koma bwanji ayambe wathana ndi mkazi wake asanabwere kwa iwe? Osapusitsidwa kuti mwakongoletsa; ayi ndithu, mwangophweka. +Adatengera Lucky Dube: Liwonde Chibwe Oimba akubadwirabadwira mdziko muno. Mmodzi mwa oimba omwe adza ndi mkokomo ndi MacDonald Liwonde Chibwe wa ku Mponela mboma la Dowa koma watambalala mumzinda wa Blantye. DYSON MTHAWANJI adacheza ndi katswiriyu motere: Wawa, tidziwane Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Chibwe: Mulungu ndi wachikondi Ndine MacDonald Liwonde Chibwe, ndimachokera mmudzi mwa Chimbudzi, mfumu yandodo Mponela mboma la Dowa. Mbanja mwathu tidabadwa ana asanu ndi awiri ndipo ine ndi wachisanu. +Ndibenthulire chiyambi cha maimbidwe ako. +Chidwi changa pa maimbidwe chidabadwa pomwe ndidali wamngono. Kuyambira ndili wamngono ndakhala ndikukonda kumvera nyimbo zakunja komanso zamdziko mommuno. Lucky Dube wa ku South Africa ndi Lucius Banda wa kuno ku Malawi ndiwo adandipatsa chidwi kuti ndikhale ndi loto lodzakhala woimba. Mchaka cha 2013 ndidajambula chimbale changa cha nyimbo choyamba chotchedwa Lingakome. Nyimbo zambiri mchimbalechi zikuseweredwabe pawayilesi zambiri ndipo anthu akuzikonda. Zina mwa nyimbo zili mchimbalechi ndi Facebook, Kadende, Hello komanso Mama Africa kungotchulapo zochepa. Zambiri mwa nyimbozi zili mchamba cha reggae. Kapekedwe kanga ka nyimbo kamagwirizana ndi chamba chimenechi. +Oimba ena oyamba kumene sachedwa kufooka ndipo amazilala msanga. Iwe suchita chimodzimodzi? Kuimba kuli mmagazi anga kotero ine ndabwera kudzakhazikika pa maimbidwe. Anthu ambiri andilandira pa nkhani ya maimbidwe. Izi zikundipatsa mangolomera kuti ndikhazikika palusoli ndipo sindikubwerera mmbuyo. Pakalipano ndikujambula chimbale chachiwiri chomwe dzina lake ndi Tingathe. Chimbalechi chanyamula uthenga womwe ukugwedeza Amalawi kuti adzuke ndi kuyamba kukonda dziko lawo komanso kugwira ntchito molimbika kuti tithetse mavuto a zachuma omwe tikukumana nawo. Pakalipano ndajambula nyimbo zinayi zomwe zipezeke mchimbale chimenechi. Nyimbozi ndi Namondwe, Dona, Ndimtima komanso True Love. Nyimbo zinayizi zikuseweredwa kale pawayilesi, komanso zikuchita bwino mupologalamu ya MBC Top 20 pa MBC Radio 2. +Chifukwa chiyani nyimbo zako zambiri zanyamula uthenga wachikondi? Mulungu ndi wachikondi ndipo sitingalekanitse Iye ndi chikondi. Ngati pali chikondi pakati pa anthu awiri pamalopo pamakhala mtendere. Kotero ndidachiona chofunika kulalikira chikondi kudzera mnyimbo zanga. +Boston Kabango: Chikhomo cha Wanderers Kungomva za Boston Kabango, omwetsa zigoli a matimu ena amayamba kunjenjemera kaamba ka ntchito za mnyamatayu zomwe amazionetsa ku Mighty Be Forward Wanderers komanso ku Flames Under 20. Kodi ntchito zake nzotani? Adayamba bwanji? Nanga tsogolo akuliona bwanji? BOBBY KABANGO akucheza naye motere: Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mpira si dzitho: Kabango Kodi Boston amamveka uja ndiweyo? Ndine ndithu, musaderere ndi maso okha koma muzipita pabwalo kuona luso lomwe Mulungu adapereka. Dzina langa lonse ndi Boston Bosnho Kabango. +Thupi limeneli umatha kulimbana ndi osewera amatupi awo? Nchifukwa ndikuti musaderere, mpira si kukula thupi koma kukhala ndi mphamvu za mpirawo. Ine ndimayesetsa kuti ndizichita mafizo kuti ndikhale ndi mphamvu zosewerera mpira, osati zoti anthu azindiona nazo. +Kodi udayamba liti kusewera mpira? Luso lidaoneka ndikusewera ku Sporting Leopards mu 2010. Titapita kukapikisana nawo kumpikisano wa Zone 6 anthu adagoma ndi luso langa ndipo Azam Tigers idanditenga. Mu 2015 mpamene ndimabwera ku Nyerere. +Moyo ku Nyerere uli bwanji? Zonse zili bwino, pena tikhumudwe pena kusangalala ndimo moyo umayendera. Kungoti pakati ndidali wovulala ndiye ndatenga nthawi osasewera, pano ndabwereramo. +Uli ndi zaka zingati? Pajatu mumabera zaka anyamata a mpira inu Hahaha! Ayinso osati kubera koma ndili ndi zaka 20. +Maphunziro ndi otani? Nanga uchitanso ziti kupatula mpira? Ndadutsa fomu 4 moti ndikufuna ndipange za umekaniki koma posakhalitsapa ndipitanso kusukulu. Ndimafunitsitsa ntchitoyi kupatula kuti Mulungu adandidalitsa ndi luso la mpira. +Umalota utadzafikira pati? Kukasewera ku England, ilili ndiye loto ndikamasewera mpira. +Ndani amakudolola? Nanga ukafatsa umakonda chiyani? Limbikani Mzava komanso kunja ndi Gary Cahill. Ngati sindikusewera mpira ndiye ndimakonda kuonera makatuni komanso kucheza ndi mayi anga. +Msika wa ziwala, mbewa Tidali pamalo aja timakonda pa Wenela, mnyamata uja Bonny Wasawaliya Kanindo atafika ku nyumba ya ulemu ku Nyumba ya Malamulo komwe adakakwanitsa kupereka chikalata chodzudzula zophana. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndinakaperekera chikalatacho mchimbudzi chifukwa ndimafuna ndikapereke ndili chinochino. Zatheka, adatero Kanindo. +Koma ayi ndithu mwaitha, uthenga wamveka ndipo tikudziwa amene amakonza zionetsero nkumayenda okhaokha atangerapo phunziro, adatero Abiti Patuma. +Kanindo adati tisachedwe pamalopo, koma titsagane naye kupita ku Limbuli komwe amafuna akakhale limodzi ndi Moya Pete amene amati akakambe za chimanga chimene chimapezeka kwambiri. +Mwayi wathu ndi womwewu, tikaguleko chimanga chifukwa pa Wenela chimanga ndiye chadula. Mwati pofika December sichikwana K25 000? Chongofika pa Limbuli, tidapeza atate, akazi awo ndi ana awo akudikira Moya Pete yemwe nthawiyo akumwa tiyi pamwala uja ankawerengera Chilembwe ku PIM mboma la Chiradzulo. +Anthu adamupatsa molalo Kanindo. Koma tidaona akuluakulu ena akulozerana zala. +Atafika Moya Pete, kudaterera. Ndidamuona akunongoneza mmodzi mwa asirikali ake. Kenako adamuloza Kanindo. +Ndidangoona asirikali aja akukhamukira kwa Kanindo, kodi kapena dzina lake ndi Kawindo? Iwe uchoke pano. Moya Pete akuti akufuna achite zisudzo aseketse anthu chikhakhali. Zisudzo unachita iwe zabunobuno zija akuti wachepa nazo, adamuuza. +Padalibe zaulemu, adamukoka kumutengera kugalimoto yake yolemba Wikoni 1. +Moya Pete adaimirira. Kumanja kwawo kudali nsalu ya mtundu wa thambo. +Inu! Inu! Mumadziwa za dirama kwambiri inu? Inetu ndidali wadirama kalelo. Zisudzo si nkhani. Mr Bean, Trevor Noah, Anne Kansiime mukutamayu, Teacher Mpami what? Onsewo ndaphunzitsa ndekha, adayamba motero. +Anthu onse adafa nalo phwete! Sindikudziwa ngati amaseka zimene amanena Moya Pete kapena amawaseka! Ndikuuzeni kwambiri! Tiyeni tizidya utakafumbi! Tiyeni zithuli zagundikazi tisazilekerere. Tasekani kwambiri, adatero. +Anthu adaseka. Ha! Ha! Ha! Abiti Patuma amvekere: Ki! Ki! Ki! Lol! Moya Pete adamezera malovu. +Inutu mukudziwa kwambiri. Chimanga chikupezeka kwambiri kuno ku Limbuli kokha kuno. Choncho, tiyeni tizingotafuna akapuko.amkokamadzi. Mukapezanso makoswe mukhoza kuchita nawo, samapha konse. Sekani kwambiri anthu inu! adapitiriza. +Anthu adaseka chikhakhali. Sindinaone munthu wodziwa kuseketsa ngati Moya Pete! Choncho! Ndachotsa chimanga chija adaika mkulu uja Mfumu Mose chifukwa pano chikusowa. Mbewa ndi zithuli ndizo tiziike apa! Muzidya zimenezi. Mwamva kwambiri? adafunsa. +Pomwe amatero nkuti akutambasula nsalu yatsopano ija. +Ndikumbuka bwino lomwe gogo uja adandipeza ndikulima osavala ankakonda kunena kuti safuna anthu ake azigona mnyumba zothonya mvula ikamagwa, azidya ndi kuvala bwino; ndidakumbukanso Mpando Wamkulu akunena kuti mukamva njala kaya minkhaka zitafunani. +Kodi tsono enatu sadya mbewa ndiye azidyanji? ndidafunsa. +Idali nthawi ya buleki Sukulu iliyonse imakhala ndi nthawi yopumira kapena kuti nthawi ya buleki. Ena amakangosewerako, ena amakadya, koma Paul Chidale ndi Dolica Mchenga adasinthana Chichewa. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Paul Chidale ndi katswiri wosewera golf komanso akugwira ntchito ku Gestetner ngati ICT Engineer. Dolica ndi wabizinesi. +Kukumana kwawo sikukugwirizananso ndi ntchito yawo chifukwa adakumana onsewa ali pasukulu ku Bangwe Private School mumzinda wa Blantyre. +Paul akuti panthawiyo adali fomu 3 pamene Dolica adali fomu 1. Iwowa adakhala akuponyerana maso, koma zonse zidakathera kubuleki. +Paul kusayinira kuti watengadi Dolica patsiku lodalitsa ukwati wawo Timaponyerana maso mosonyeza kuti timafunana. Tidapezera mwayi nthawi ya buleki pamene tidakumana ndi kucheza, adatero Dolica. +Adati akundifuna, koma ndidavutavuta ngakhale pansi pa mtima nanenso ndimamufuna Paul. Kungoti Paul amandisangalatsa machezedwe ake ndi anthu komanso malankhulidwe ake opatsa chikoka, adaonjezera. +Paul akuti padatenga kanthawi kuti amumasule Dolica ndi mawu akukhosi chifukwa amafuna aone ngati namwaliyu adali ndi makhalalidwe abwino. +Zooneka bwinozo ndiye musakambe, namwaliyu ali bwino komanso ndimafuna kuonetsetsa makhalalidwe ake. Nditakhutira, ndidaganiza zomupezera nthawi ndipo kudali kubuleki komwe ndidakamuuza mawu anga, adatero Paul. +Izitu ati zimachitika mwezi wa April mu 2007. +Ukwati ndiye adamanga pa 4 October 2015, ku Feed the Children ku Nyambadwe mumzindawu. +Amene sadakwatire afatse kaye chifukwa ukwati weniweni umachitika kamodzi pamoyo wa munthu mpaka Mulungu adzakulekanitseni. Ndiye akuyenera atsimikizedi za yemwe akufuna amukwatire kapena kuwakwatira, adatero Paul wa mmudzi mwa Luwanje kwa T/A Chikumbu mboma la Mulanje, polangiza omwe akulingalira za banja. +Kamuleni ndi Polisi Palibe Tsikulo nkhani idavuta ndi ya anyamata ena aja adabutsa bwalo la milandu mtaunimu. Adaganiza bwanji anthuwa? Uku nkugenda kupolisi wamkulu fodya ali mthumba la kumbuyo. +Kukhala mavuto, anthu tsopano aziyenda kuchoka ku Chirimba, Ndirande ndi Chilomoni kupita kuja koonekera ku Chichiri. Yalakwa, adatero Abiti Patuma. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Apatu khoswe ali pamkhate koma ndani angaope kuswa mkhate lero? Ndani lero angaloze kuti uwo ndi mkhate? Kuuswa basi! Tisachedwe ndi anyamata olangika ndi zotsatira za mkalabongo. Nkhani idazunguza anthu pa Wenela ndi ya zochitika ku Polisi Palibe, gulu la masiye. +Ndikumva kuti nkhani ikuvuta ndi ya kulimbana pankhani ya Kamuleni Kaduwa komanso Udadili Issa omwe anenetsa kuti libolonje lalowa ku Polisi Palibe kuchokera ku Dizilo Petulo Palibe, adatero Gervazzio, wapamalopo. +Abodza amenewo. Kodi onsewo ndimayesa adali ndi zipani zawo lero akudzetsa mpungwepungwe kwa Adona Hilida. Kodi Kaduwa suja adazunguza Mpando Wamkulu ndi PDM yake? Nanga uyu Issa sankati tonse ndi Amaravi? adayankha Abiti Patuma. +Abale anzanga, musandifunse kuti ankatanthauza chiyani chifukwa sindikuuzani. Ndipo mukadziwa mukufuna mutani? Nthawi yomweyo, Gervazzio adaika nyimbo ya San B komanso Nepman, inde nyimbo imene adaimba uja mnyamata wa ku Chileka. +.Amatigoneka kukada Amatidzutsa kukacha Amatidyetsa tikamva njala Ili ndi pemphero limene lalowerera paliponse pamene kulira ndi njala kwafika pena. Kugona kumsika kuti ugule chimanga, kuotha dzuwa komweko mpaka nthawi ya nkhomaliro opanda chakudya. +Ndimakumbuka tsiku lina titamupanikiza Moya Pete kuti atifotokozere bwino za mmene abweretsere chakudya pano pa Wenela. Mmalo mwake adati: Amalawi tikutukwanana kwambiri pa Facebook. Tikuphana osati masewera kwambiri. +Koma ine ndikuona ngati kuimbanso nyimbo za Michael Jackson kapena Bob Marley nkutaya nthawi. Adaziimba bwino kale, adatero Gervazzio. +Palibe uyo adayankhira nkhani imeneyo chifukwatu maimbidwe ali mmagulu. +Tili pa Wenela chomwecho adatulukira Fula Kasamba. Tonse chimwemwe chidadzala tsaya. Koma abale, kuphwetsana madzi kotereku bwanji? Walakwanji munthu? Ndatulukamo motenthamo. Iwe Tade usandilankhule, sindikufunanso kupalamula. Zoona tsiku ngakhale limodzi osabwera kudzandiona? Ufiti wako udafika pamenepo? adafunsa Fula. +Mudalinji mchakachi? Ma alubino aona zakuda Mpotopola ku Joni, Amalawi 3 200 athothedwa Anthu 106 afa ndi madzi osefukira Tili mchaka china, 2015 wapita ndipo talowa 2016. Lero tikhale tikuunguza zina mwa nkhani zikuluzikulu zomwe zidamera nthenje mchaka changothachi. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Maalubino aona mbonaona Kwa nthawi yoyamba, dziko lino lidaona zomwe zakhala zikungomveka mmaiko ena. Mchaka cha 2015 taona maalubino akusakidwa ngati nyama. Kuwapha, kuwachotsa ziwalo, komanso kuwagulitsa kumene pokhulupirira kuti ziwalo zawo zingabweretse chuma. +Mchitidwewu udatenga malo ku Machinga, Balaka, Dedza komanso Mangochi. Nkhaniyi yakhala ikudandaulitsa bungwe lomenyera ufulu wa anthuwa la Association of People with Albinism in Malawi (Apam) malinga ndi mkulu wa bungweli, Boniface Massah. +Massah adati zonsezi zakhala zikuchitika chifukwa cha zilango zomwe mabwalo akhala akupereka kwa yemwe wapezeka wolakwa. Mwachitsanzo, mboma la Dedza amayi ena adalamulidwa kukaseweza kundende zaka ziwiri atapezeka olakwa pankhani yofuna kusowetsa alubino, nkhani yomwe idadandaulitsa bungweli. +Mwezi wa March, anthu achialubino pamodzi ndi mabungwe adachita zionetsero mumzinda wa Blantyre pofuna kuonetsa mkwiyo wawo ndi zomwe zakhala zikuchitika. +Mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, adalonjeza kuti athana ndi onse amene apezeke olakwa komabe ngakhale adalankhula motere, anthuwa akhalabe akukhala mobisala mdziko lawo lomwe. +Madzi osefukira, anthu 106 afa pangozi za madzi Pa 19 January chaka changothachi, ngozi idachitika mmaboma 15 mdziko muno pamene madzi a mvula yosakata adasefukira ndipo maboma a Nsanje, Mulanje ndi Chikwawa ndiwo adakhudzidwa kwambiri, komanso maboma ena monga Rumphi ndi Karonga kumpoto. +Ngoziyi idachitika chifukwa cha mvula yomwe idagwa yochuluka mdziko muno kwa sabata ziwiri osalekeza. +Anthu 145 000 adakhudzidwa mmaboma 6 ena adasamutsidwa mmalo mwawo ndi kukasungidwa mmisasa. +Anthu 106 adafa pangoziyi ndipo dera lokula ndi mahekitala 64 000 lidakokoloka. Kutsatira ngoziyi, matenda a kolera adabuka ndipo anthu 423 adakhudzidwa ndi matendawa omwe adapaha anthu 6. +Mutharika adalengeza kuti dziko lino ndi malo angozi ndipo kotero mabungwe ndi maiko akunja akuyenera kupulumutsa dzikoli kumavutowo. Mawuwa adachititsa kuti mabungwe akunja koma ena a mdziko la Malawi momwemuno ayambe kupereka thandizo losiyanasiyana kwa anthu amene adakhudzidwa. +Mtopola ku Joni, Amalawi athothedwa Nkhani inanso yomwe idakula mchakachi ndi zipolowe zomwe zidabuka mdziko la South Africa kuchitira alendo amaiko ena amene akugwira ntchito mdzikomo. +Maiko adayamba kusamutsa nzika zake mdzikolo chimodzimodzinso dziko la Malawi mu April lidasamutsanso nzika zake 3 200 zomwe zidakhudzidwa ndi mtopolawo. +Mtopolawo udali wachiwiri dziko la South Africa likuchitira alendo amene akudzafuna maganyu mdzikomo. Mu June 2008, dziko la South Africa lidachitiranso mtopola alendo a mmaiko ena amene akukhala mdzikolo ndipo anthu 60 adaphedwa pamene anthu oposa 600 adavulazidwa. +Lero pamene mwachita bata mdzikomo, Amalawi ambiri akhamukiranso mdzikomo kukafuna maganyu. +Ziwawazo zidayamba pamene mfumu ya Mazulu Gooodwill Zwelethini idakolezera moto ponena kuti nzika za mmaiko ena zibwerere kwawo ati chifukwa zikuwaphangira ntchito. +Ngakhale utsi sufuka popanda moto, Zwelethini adakana izi ponena kuti atolankhani ndiwo sadamumvetse. +Maiko komanso mabungwe mu Africa adadzudzula zomwe zochitika mdzikolo. +Dziko la Nigeria nalo lidayamba kusala nzika za dziko la South Africa. Ku Zimbabwe, mawailesi a mdzikolo adayamba asiya kuimba nyimbo za mdziko la South Africa, pamene ku Mozambique, nzika zina za mdziko la South Africa zidachitidwa chipongwe. +Ku Malawi kuno anthu adachita zionetsero pamene adakapereka chikalata cha madandaulo awo kwa kazembe wa dziko la South Africa. Kuphatikiza apo, Amalawi adachitanso zionetsero zina zokakamiza kuti anthu asamagule katundu msitolo za mdziko la South Africa zimene zili mdziko muno monga Shoprite, Game ndi Pep. +Boma lichotsa mafumu amtauni Nkhani ina yomwe idazunguza mchakachi mpaka lero ndi ya ganizo la boma lofuna kuchotsa mafumu mmizinda, mtauni komanso mmamanisipalite. +Unduna wa maboma angono ndiwo udatulutsa chkalata chomwe chidadzetsa kusagwirizana pamene mafumuwo adaopseza boma kuti achita zomwe angathe pofuna kuteteza ufumu wawo. +chikalatacho mwa zina, chidati mafumuwo sazilandiranso mswahara chifukwa tsopano ndi anthu wamba. Gawo 3 (5) la malamulo okhudza ufumu (Chiefs Act) ndi lomwe lidaomba mkota paganizo la bomalo. +Mafumu a mizinda ya Lilongwe, Mzuzu, Zomba ndi Blantyre komanso manisipalite za Luchenza ndi Kasungu, ndiwo adakhudzidwa ndi chikalatacho. +Nkhaniyi itafika pampondachimera, boma lidabweza moto ndipo mafumuwa akugwirabe ntchito yawo monga kale. +Boma liletsa masacheti Mchaka chimenechi dziko la Malawi lidabwera ndi ganizo loletsa mowa wa mmasacheti. +Msonkhano wa nduna za boma udavomereza zoletsa mowawu ndipo kwangotsala kuti pakhale lamulo lokakamiza aliyense kusiya kugulitsa mowawu. +Kudali ku sitolo ya Peoples Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Khalidwe la Gift Simkonda lokonda kukagula katundu kusitolo ya Peoples kwa Magalasi ku Ndirande mumzinda wa Blantyre mchaka cha 2010 lidathera kwa mnyamatayu kuzulamo nthiti yake, Eunice Chingoni. +Panthawiyo nkuti Eunice akugwira ntchito ya pa till msitolomo pamene Gift adali akugwira ntchito ku sitolo za Dapp ngati wophunzitsa anthu za mmene angamachitile malonda ku Ndirandeko. +Malinga ndi Eunice, nthawi zonse akaona Gift akulowa musitoloyo, mtima wake umakankha mwazi mwaliwiro kulakalaka mnyamatayu atadzakhala wakumkeka wake koma poti ndi mkazi sakadalankhula kotero amayesetsa kumuchitira mkomya musitolo momwemo pomudindira komanso kumulongezera mnyamatayu katundu bwino mujumbo akagula katundu. +Banja la Simkonda tsiku la ukwati Zinkandiwawa Gift akapita podinditsira mitengo pamunthu wina chifukwa ndinkadziwa kuti sindimva mawu ake komanso sandiona, adatero Eunice. +Iye adati, chimene chinkamuzula moyo kwambiri mwa Gift ndi lilime lake la Chitumbuka, maonekedwe ake ofatsa komanso kuumbidwa bwino kwa mnyamatayu. +Naye Gift adati mtima wake udayamba kuthawathawa mmalo ngati netiweki ya lamya za mmanja atasiyanitsa umunthu umene nthandayi idali nayo pa makasitomala kufikira pamene naye adayamba kudyerera maso padonalo. +Gift adati kupatula kudzichepetsa komanso nsangala zimene zidakuta wakumkeka wakeyu, mnyamatayotu akutinso ankakopeka ndi dzino logamphuka limene lili mkamwa mwadonalo limene limaonekera akamamwetulira. +Nditayizindikira nyenyeziyi sindidachedwe koma kupatsana nayo nambala ya foni ndipo patadutsa masiku tidagwirizana kuti tikumane kuti ndikatule nkhawa zanga pa iye, adatero Gift. +Koma Gift akuti adakhumudwa ataponya khoka lake la chikondi mudziwe la chikondi la njoleyi pamene duwali lidatemetsa nkhwangwa pamwala kuti silikufuna kugwa mchikondi ndi iye. +Ndidakana dala ngakhale pansi pamtima ndinkadziwa kuti ndikumufuna. Ndinkafuna kuonetsetsa kuya kwa chikondi chake paine ndipo pakutha pa miyezi iwiri ndi pamene ndidampatsa makiyi a mtima wanga, adatero Eunice. +Nkhani ya awiriwa itafika mmakwawo kuti akufuna akwatirane idautsa mapiri pachigwa chifukwa akwawo kwa Eunice, mngoni, sankafuna akwatirane ndi mtumbuka ndipo akwawo kwa Gift sankafuna kuti mwana wao akwatirane ndi mngoni. +Awiriwa adati zidali zopweteka kwambiri ngati dzino lobooka kuzimvetsetsa kuti asakwatirane chifukwa cha kusiyana chilankhulo ndi mtundu. +Pafupifupi chaka chinadutsa anthu akwathu atatisiyanitsa koma sitidakhale chete tidayetsetsa kuwaunikira kuti chikondi adalenga ndi Mulungu ndipo Mulunguyo ali ndi mphamvu yolumikizanitsa anthu amitundu yosiyanasiyana ndikukhala thupi limodzi. Tidali okondwa anthu ambali zonse ziwiri atatimvetsetsa ndikutilola kuti titengane, adatero Gift. +Awiriwa adamangitsa woyera pa August 4 2013 ndipo ali ndi mwana mmodzi, Wongani, amene akwanitse chaka chimodzi chaka chino. Banjali likukhala ku Zomba kumene Eunice akugwira ntchito ku sitolo ya Peoples ya Matawale pamene Gift akugwira ku Dapp ya mumzinda wa Zomba. +Ulendo womaliza wa Grace Chinga Thupi la Grace Chinga yemwe adamwalira Lachitatu usiku liikidwa lero mmanda a HHI mumzinda wa Blantyre. +Thupi la Grace limayembekezeka kutengedwa kunyumba yachisoni ku College of Medicine dzulo masana ndipo lero cha mma 8 koloko thupi lake likuyembekezeka kutengedwera ku Robins Park komwe kukhale mapemphero komanso oimba anzake akhala akuimba pomukumbukira. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Adatisiya Lachitatu: Chinga Malinga ndi malume ake a Grace, mbusa Isaac Mpasula, kuchokera ku Robins, ukakhala ulendo wa ku HHI komwe woimbayu akagone. +Pokambapo za chomwe chidapha Grace, Mpasula adati woimbayu amakhala ku Chilobwe ndipo sabata yatha iye adasamuka kukayamba kukhala ku Machinjiri ku Area 7. +Tsiku lomwe adangofika ku Machinjiriko, adaimba foni kwa mayi ake kuwadziwitsa kuti wafika bwino koma wangofikira kudwala. +Adawauza kuti akudwala mutu, koma malinga ndi kufotokoza kwawo, sizimaonetsa kuti matendawo adali akulu, ndipo ife timati tipitako tsiku lina kuti tikaone komwe akukhala, adatero Mpasula. +Iye adati pamene nthawi idali cha mma 6 koloko madzulo a Lachitatu, adaimbiranso foni mayi akewa kuwadziwitsa kuti Grace wakomoka koma apo amaimba ndi mwana wake wa Grace. +Tisadanyamuke tidangomva kuti amutengera kuchipatala. Cha mma 9 koloko tikulandira uthenga kuti Grace wamwalira. adatero mosisima. +Pamene timalemba nkhaniyo nkuti zotsatira za chipatala zisadatuluke kuti apeze chomwe chidapha woimbayu. +Mbiri ya Grace Chinga Grace adabadwa pa 28 June 1978 ku chipatala cha Gulupu. +Grace ali moyo amati mtundu wawo udachokera mdziko la Mozambique mmudzi mwa Chinga. Pamene adalowa mdziko la Malawi, bambo ake amakhala mboma la Thyolo pamene mayi ake ndi a ku Chikwawa. +Iye wakulira ku Chimwankhunda mumzinda wa Blantyre ndipo amapemphera mpingo wa Full Gospel womwe udayambitsidwa ndi bambo ake amenenso adamwalira. +Grace adakwatiwapo ndi Rodgers Moffat ndipo chithereni cha banja lake, iye sadakwatiwenso. Iye wasiya ana atatu: Steven, Miracle ndi Israel. +Kumbali yoimba, Grace adayambira ku kwaya ya kumpingo kwawo. Iye adalowanso gulu la All Angels Singers komanso Glad Tidings mzaka za mma 1996. +Mu 2002 iye adatulutsa chimbale chake choyamba cha Yenda mu 2002 momwe mudali nyimbo zotchuka monga Uleke, Ndagoma, Timveke Maluwa ndi zina. +Kudziwika kwenikweni idali nthawi yomwe adatulutsa chimbale cha Ndiululireni momwe mudali nyimbo ngati Akadapanda Yehova, mu 2011. +Nyimbo zomwe anthu akhala akuimba msabatayi ndi monga Kolona yomwe mbali ina imati Ndinabwera ndi mission, Ndinatumidwa ukazembe, ntchito ikadzatha. Ndi pamene ndidzaweruke, Palibe ondileketsa ntchito yanga ili mkati, kufikira mwini wake adzanene kuti amen. +Grace wamwalira akuphika chimbale chatsopano momwe muli nyimbo imene adangoitulutsa ya Ndzaulula. Polankhula asadamwalire, Grace amati chimbalechi chituluka mu June mwezi womwe adabadwa. +Lero Grace wayalula monga mwa nyimbo yake ndipo maso a anthu akhale pa mwana wake Steven amene watulutsa nyimbo ya Udzandikumbuka. +Mmodzi mwa oimba amene adzamukumbuke Grace ndi Ethel Kamwendo chifukwa cha chinthu chimodzi chomwe Grace adamulonjeza Ethel adakali moyo. +Adanena kuti ndikamakajambulitsa chimbale china, iyeyo adzandipatsa nyimbo ponena kuti nyimbo imeneyoyo ineyo ndi amene ndingathekuimba. Zachisoni Grace wapita osakwaniritsa lonjezo lake, adalira Ethel. +Escom ikhazikitsa ntchito yatsopano ya magetsi Boma kudzera ku bungwe la magetsi la Electricity Supply Corporation of Malawi (Escom) lakhazikitsa pulojekiti yotchedwa Ndawala yobweretsa magetsi kumidzi pofuna kukweza chiwerengero cha anthu ogwiritsa ntchito magetsi mdziko muno. +Ntchitoyi cholinga chake ndi kufulumizitsa kulumikizira anthu magetsi mmadera akumudzi komanso mmatauni pangongole yopanda chiwongola dzanja ya ndalama zokwana K75 000, yomwe idzakhale ikuperekedwa pangonopangono podula K20 pa K100 pamagesti olipiriratu a Escom. +Goma comes out of cocoon Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Kudzera mu ntchitoyi, yomwe ndi yandalama zokwana K350 million, bungweli likumaikira lokha mawaya munyumba za anthu omwe akumayenera kupereka ndalama zokwana K5 000 kuti awalumikizire magetsi. +Poyankhula pa mwambo wkhazikitsa ntchitoyi ku Ntcheu, Nduna ya zachilengedwe, zamagesti ndi zamigodi, Bright Msaka, adati ndondomekoyi ithandiza Anthu ambiri kupeza magetsi mdziko muno, makamaka madera amene anthu ena sangathe kupeza ndalama zokwanira kuikira mawaya ndinso kulumikiza magetsi. +Chifukwa cha chitukuko cha magetsiwa kuno kumudzi, ntchito zambiri zomwe timachita kukwerera basi kupita kutauni, anthu ambiri tizitha kuchitira konkuno kumudzi. Izi zizapangitsa kuti anthu ambiri athe kupeza ntchito komanso kuyambitsa mabizinesi konkuno kumudzi, adatero a Msaka. +Iye adawonjeza kunena kuti izi zidzachepetsa nthawi imene anthu amataya posakasaka makontilakita komanso kuyendera maofesi a Escom. +Mmawu ake, wapampando wa bungweli, Jean Mathanga, adapempha anthu omwe apindule kudzera mu ntchitoyi kuti asamalire zipangizo zamagesti kuti chitukuko chimenechi chifalikire mmadera ambiri mdziko muno. +Mukapeza munthu akuononga zipangizozi, chonde tiuzeni kapena kanenei kupolisi ngakhalenso kwa atsogoleri a mmadera mwanu. Komanso tikapeza waya wa Escom atagwa pansi tiyeni tiwauze a Escom kapena kupanga lipoti kupolisi mwansanga, adatero Mathanga. +Imodzi mwa mafumu ku Ntcheu, Inkosi Chakhumbira, idati ndi yokondwa kwambiri ndi ntchitoyi ponena kuti ilimbikisa ntchito zamalonda, kuthandizira poteteza zachilengedwe komanso kukhwimitsa chitetezo mbomalo. +Aletsa zionetsero ku Nkhata Bay Gulu la anthu omwe amakonza zionetsero zofuna kukakamiza boma kuti likonze msewu waukulu wopita ku Mzuzu, limange msika komanso malo oimira basi mboma la Nkhata Bay lidagwetsa ulesi anthu Lachitatu lathali pomwe zionetserozo zidalephereka mwadzidzidzi. +Makomiti atatu a zachitukuko mmadera a ma T/A Timbiri, Mankhambira ndi Mkumbira ataona kuti zitukuko zikuchedwa kukwaniritsidwa mbomalo, adagwirizana zochita chionetsero ndi kukapereka chikalata ku ofesi ya DC wa bomalo. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Gululo lidagwiritsa ntchito gawo 30 la malamulo oyendetsera dziko lino omwe amakamba za ufulu wa anthu pachitukuko. +Koma tsiku la zionetserozi litafika, anthu adauzidwa kuti bwanamkubwa (DC) wa bomali sadapereke chilolezo ndipo ngati anthuwa angapitirire ndi zionetserozi zikhala zosaloledwa. +Kaunda: Ngati sakutiuza zomveka tipitirira ndi zionetsero Ena mwa anthu omwe amafuna kutenga nawo mbali pazionetserozo adadzidzimuka atauzidwa atafika kale pamalo a nkhumano kuti zionetserozo zalephereka. +Nawo apolisi ovala zamawangawanga omwe adalipo 16 sadalekerere koma kuchoka mumzinda wa Mzuzu kukasonkhana nawo pamalo a nkhumanowo pa roadblock yaikulu mbomali. Koma patatha maola awiri opanda chochitika adabwerera ku Mzuzu. +Mneneri wa polisi mchigawo cha kumpoto, Maurice Chapola, adati apolisiwo adangopita kukakhala tcheru posungitsa bata ngati zionetserozo zikadapitirira. +Msangulutso adalankhula ndi wampando wa komiti yomwe imakonza zionetserozi, Mabvuto Kaunda, yemwe adati bwanamkubwa wa bomali ndi amene adaletsa zionetserozi. +Monga mwa malamulo a dziko lino zionetsero zimachitika pokhapokha ngati padutsa masiku awiri mutapereka kalata yanu yodziwitsa DC. Ife tidatsatira izi bwino lomwe chifukwa tidapereka kalata yathu Loweruka sabata yatha kuwadziwitsa kuti tichita zionetsero Lachitatu, adatero Kaunda. +Koma Kaunda adati adali odabwa atauzidwa ndi DC Lachiwiri kuti zionetserozo sizikhalako kaamba koti Lolemba lidali latchutchi choncho sangaliwerengere. +Ifetu zionetsero zathu zikadakhala za bata ndipo timafuna kukapereka kalata kudzera ku ofesi yawo yopita kuofesi ya mtsogoleri wa dziko lino yoti ngati satiyankha zakuspa pamasiku 30, tidzayamba kugona kuofesi ya bwanamkubwayu, adatero Kaunda. +Iye adati anthuwa atopa ndi kulonjezedwa zitukuko zomwe sizikukwaniritsidwa. Kaunda adati ngakhale boma lidayamba kulonjeza zoti likonza msewuwu ndi ndalama zochokera ku bank ya African Development Bank (AfDB) zaka zapitazo, pamalopa palibe ndi kontilakita yemwe. +Tidamvetsedwanso kuti kudaperekedwa K368 miliyoni yomangira depoti ndi msika, koma zonsezi kuli zii, adadandaula Kaunda. +Iye adati bwanamkubwayu wauza komitiyi kuti a unduna wa za mayendedwe komanso bungwe loona za misewu mdziko muno la Roads Authority (RA) akumana nawo kuti athetse kusamvanaku. +Koma ife tikuti, ngati sakatiuza zomveka, tipitirira ndi zionetsero, adatero Kaunda. +DC wa bomali, Alex Mdooko, sadapezeke pa lamya zake zonse ziwiri pomwe timasindikiza nkhaniyi. +Koma mneneri wa bungwe la RA, Portia Kajanga, adavomereza kuti ntchitoyi yachedwadi. Iye adati koma apa nguluwe yalira msampha utaninga chifukwa ati ntchitoyi iyamba posachedwappa. +Ntchito yatha kale, inde tachedwa koma anthuwa asade nkhawa, zitheka osati chifukwa atiopseza koma potsatira dongosolo lake, adatero Kajanga. +Ntchito yomanga msewu idakhazikitsidwa mwezi wa July mchaka cha 2013 ndipo panthawiyo ntchitoyi imati itenga ndalama zokwana K14.8 biliyoni ndipo imayembekezereka kugwiridwa kwa zaka zinayi mpaka chaka cha 2017. +Aphungu asaiwale kukambirana za njala Pomwe kwangotsala masiku 9 kuti aphungu a ku Nyumba ya Malamulo akakumane kukambirana za momwe ndondomeko ya chuma yayendera pa miyezi 6 yapitayi, mabungwe ndi mafumu ena ati nkhani ya njala isakalephere kukambidwa. +Mabungwe ndi mafumuwa ati nkhani ya njala ili mkamwamkamwa paliponse kotero kuti ikufunika kupatsidwa mpata aphunguwa akamakumana kuti papezeke njira zothandizira anthu, makamaka a mmidzi. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Chifukwa cha njala ena akuupeza pa nyanya kapena nyika Mfumu yaikulu Mkukula ya ku Dowa yati kupanda kukambirana za njala ndiye kuti palibe chimene msonkhano wa aphunguwo ungaphule. +Panopa ngakhale mwana wamngono akudziwa zoti njala yayamba chifukwa amazionera mnyumba mwawo kuti zinthu sizikuyenda momwe zimakhalira nthawi zonse, idatero mfumuyo. +Iyo idati mmisika yambiri ya Admarc chimanga chikuvuta kupeza moti anthu akuchita kugonera komweko kapena kulawirira kuti mwina apeze mwayi wogula chakudya ndipo izi zaimitsa ntchito zambiri mmidzimo. +Mmalo molawirira kumunda kapena kudimba, anthu akulawirira ku Admarc kukadikirira chimanga. Choncho kumundako kukapanda kusamalika, chaka chamawa kudzakhala zotani? Iyi ndi nkhani yofunikira kwambiri ndipo isakalephere, adatero Mkukula. +Iye adati kupatula kukambirana zoti chakudya chizipezeka mmisika ya Admarc, aphunguwa akakambiranenso za njira zoti anthu akapanda kukololanso bwino azidzalima chakudya china monga kudzera mu ulimi wamthirira. +Pophera mphongo, mfumu yaikulu Tsabango ya ku Lilongwe idati nkhani ya chakudya ikufunika kuikapo mtima komanso njira zoti anthu azipezera chakudya china podzera mnjira ya ulimi wamthirira. +Ife mafumu ndiye timakhala ndi anthu mmidzimu ndiye chilichonse chikachitika chimayambirira kupeza ife. Ngakhale nkhani ya chakudya imene, ngati chimanga chikusowa mmisika, anthu amayangana ife, adatero Tsabango. +Iye adati pokambirana za mmene ndondomeko ya chuma cha 2015/2016 yayendera mmiyezi 6 yapitayi, mpofunika ndithu kupeza mpata wokambiranako za chakudya ndi njira zolimira mnyengo ya chilimwe kuti zinthu zisadzachite kufika posauzana. +Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a zaulimi la Civil Society Agriculture Network, Tamani Nkhono-Mvula, adati zomwe mafumuwa anena nzoona kutengera momwe zinthu zilili. +Iye adatchulapo kukwera mtengo kwa chimanga chomwe chili ndi mavenda, kusowa kwa chimanga mmisika ya Admarc ndi kabweredwe ka mvula ka chaka chino, zomwe adati sizikupereka chiyembekezo chokwanira kwa anthu. +Nkhono-Mvula adati pakufunika mfundo zomveka bwino komanso ndondomeko yooneka bwinobwino ya kagawidwe ka chimanga mmadera osiyanasiyana kuti mmadera onse anthu azitha kupeza chakudya uku akugwira ntchito mminda yawo kuti chaka chamawa asadzavutike. +Pokambiranapo, aphungu akaonetsetse kuti akhazikitsa mfundo zoteteza kuti ogulitsa chimanga mmisikayi akutsata malamulo osati kuchita chinyengo ndi mavenda omwe amafuna kuti azigula kumisikayi motsika mtengo iwo nkumakagulitsa pamtengo wokwera. +Anthu, makamaka akumidzi, akufunika chitetezo chachikulu pankhaniyi chifukwa ambiri timamva akudandaula kuti akapita mmisika amapeza chimanga mulibe koma mavenda akupezeka nacho. Iwo msika wake amaupeza kuti? adadabwa Nkhono-Mvula. +Pankhani ya ulimi wa mthirira, mkuluyu adati maganizo a mafumu ndi olondola potengera momwe mvula ikugwera chaka chino. Iye adati sizikudziwika kuti makololedwe adzakhala otani. +Nkhani ya mthirira ndiye siyochita kufuna riferendamu, aliyense akudziwa kuti njira yokhayo yolimbana ndi kabweredwe ka mvula ka chaka chino ndi mthirira basi, ndiye aphungu sangakambe za njala osakambirana za mthirira, adatero Nkhono-Mvula. +Mkulu wa mbali ya boma mNyumba ya Malamulo Francis Kasaila adati ngakhale mndandanda wa zokambirana za kunyumbayi sudatuluke, nzachidziwikire kuti aphungu akakambirana nkhani ya njalayi. +Iye adati pali nkhani zingapo zomwe zidatsalira pankhumano yomwe amakambirana za bajeti zomwe akukhulupilira kuti zibwereranso mnyumbayi ndipo nkhani ya njala ndi imodzi mwa nkhani zomwe aphungu sangalekerere kukambirana. +Anatchezera Sakuthandiza Agogo, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndine mtsikana wa zaka 21 ndipo ndili ndi mwana mmodzi. Amuna anga adandisiya ataona kuti ndili ndi pathupi ndipo mwana atabadwa adauzidwa koma mpaka pano sadabwereko kudzaona mwana wawo. Ndikawauza za chithandizo samayankha, amangozengereza. Chomvetsa chisoni nchakuti munthune ndimakhala ndi agogo okalamba poti makolo anga onse admwalira. Ndithandizeni, ndipange bwanji? JS Mulanje Pepa JS, Apa zikuonekeratu kuti ngakhale ukuti amuna anga anthunu simunali pabanja ngakhale mumagonana mpakana kuberekerana mwana. Chimene chimachitika nthawi zambiri nchakuti atsikana akangogwa mchikondi ndipo mwamuna akangowauza kuti awakwatira, basi amaganiza kuti mwamuna ndi yemweyo basi ndipo amayamba zogonana naye ati pofuna kulimbikitsa chikondi kuti asamakaike za chikondi chawo, kumene kuli kulakwa kwakukulu. Atsikana ambiri aononga tsogolo lawo chifukwa cha mchitidwe wotere chifukwa anyamata kapena amuna ambiri ndi akamberembere, ongofuna kudzisangalatsa osalabadira za tsogolo la mnzawo. Akangomva kuti mtsikhana watenga pathupi basi, chibwenzi chimathera pomwepo. Zikatero mtsikana zako zada. Koma dziko lino lili ndi malamulo okhudza maukwati ndipo ngati wina wakuchimwitsa, ali ndi udindo woti akusamale komanso mwana. Ndiye apa usazengereze-pita ukadule chisamani kukhoti basi kuti chilungamo chioneke. Mwina amuna ena amene amakonda kuchimwitsa ana a eni akhoza kutengerapo phunziro! Akundikakamira Agogo, Ndine mtsikana wa zaka 19 zakubadwa, vuto langa ndi lakuti pali mnyamata wina wake amene amandifuna koma ineyo sindimamufuna olo pangono. Iye samafuna kuti angondisiya moti pano miyezi itatu yakwana akundifunabe. Nthawi zina ndimayesetsa kuti ndimuonetse nkhope yosangalala koma mtima wanga umakana. Ndiye nditani poti ine ndili naye kale amene ndimamukonda ndi mtima wanga wonse? Chonde ndithandizeni. +MT Zomba Zikomo MT, Ndithudi akadakhalapo atsikana ambiri amaganizo ngati akowa bwenzi zinthu zikoma. Atsikana ambiri masiku ano amakonda kukhala ndi zibwenzi zambirimbiri ati kuti pamapeto adzasankhepo mmodzi. Chimenecho si chikondi ndipo mapeto ake ambiri amasokonezeka, mwinanso kutenga pathupi pa mnyamata amene samamukonda. Apa iwe waonetsa kale kuti ndiwe wokhwima mmaganizo ndipo ndikufuna kuti ndikulimbikitse kuti chikondi sakakamiza. Ngati uli kale ndi mnyamata amene umamukonda ndi mtima wako wonse palinso chifukwa chanji choti uzitaya nthawi ndi wina amene ulibe naye chidwi? Komabe nthawi zina chimachitika nchoti amene umamukonda kwambiri iye alibe chikondi, angofuna kukuseweretsa ndi kukometsa mawu a pakamwa ndipo amene sukumukonda ndi amene ali ndi chikondi chozama pa iwe. Ndiye apa chimene ungachite uyambe waona kuti bwenzi lakolo ndi munthu wotani? Ndi wamakhalaidwe otani? Ndi waulemu kapena ayi; ndi yo kapena wodzilemekeza; cholinga chanu ndi chiyani pa ubwenzi wanu? Chimodzimodzi amene ukuti akukukakamira chibwenziyo, kodi ndi munthu wotani? Cholinga chake ndi chiyani? Ndi wakhalidwe kapena mvundulamadzi chabe? Ukalingalira zonsezo bwinobwino mpamene ungasankhe chochita, chifukwatu nthawi zina umatha kukakamira mtunda wopanda madzi nkusiya munthu wachikondi weniweni. +Mafupa a alubino si chizimbasinganga Mwadzidzidzi, dziko la Malawi latchuka ndi mbiri yomvetsa chisoni komanso yochititsa manyazi. Iyitu ndi nkhani yozembetsa ndi kupha maalubino ati pokhulupirira kuti mafupa awo ndi chizimba chopezera chuma. Nkhaniyi yautsa mkwiyo waukulu kwa mabungwe, a mipingo, boma, ndi anthu ambiri omwe akuti uku nkulakwa komanso kuzunza anthu osalakwa. Ambiri amakhulupirira kuti anthu omwe akuchita izi amapita ndi ziwalo za maalubinowa kwa asinganga kuti akapangire zizimba. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi singanga wodziwika bwino mumzinda wa Lilongwe pankhaniyi motere: Mbewe: Amene akuti mafupa a maalubino ndi chizimba akunama Tidziwane wawa Escom in free-for-all fuel scam Wait gets longer Secrecy over party funders Ine ndine Dr Mustaf Socrates Mbewe wochokera mmudzi mwa Sawasawa kwa T/A Chikowi mboma la Zomba. +Chabwino apa ndakupezani muli jijirijijiri, kodi mukutani? Pano ndili pantchito yanga. Ine ndine singanga ndipo anthu ambiri amandidziwa, monga mukuonera apamu, anthu onsewa akufuna ndiwathandize ndipo si okhawa, ena athandizika ndipo apita kale. +Nkhani yabwino, komatu ine ndili ndi funso. Mdziko muno mwatchuka ndi zopha maalubino ati mafupa awo nchizimba, nzoona zimenezi? Limeneli ndi bodza lamkunkhuniza chifukwa anthu amenewa nchimodzimodzi munthu aliyense kungoti iwo ali ndi khungu loyera. Chimene chija nchilema chabe koma chilichonse ali ngati mmene munthu adalengedwera. +Nanga mukuona kuti omwe amachita izi amachitiranji? Anthu amachita izi chifukwa cha zikhulupiriro chabe. Palibe chizimba choti munthu nkumati akapha alubino ndiye kuti alemera. Zikadatero bwenzi atayamba kulemera makolo kalelo komanso si bwenzi mbadwo uno utapeza alubino ayi chifukwa bwenzi anthu atawamaliza kufuna kulemera. +Nanga poti akuti zizimbazo amapanga ndi asinganga, inu muti bwa? Ndanena kale kuti iyi si nkhani yoona, ayi, ndipo ngati alipo asinganga omwe amachita zoopsa ndi zochititsa manyazizi azindikire kuti kumeneku nkulakwa chifukwa ngakhale mawu a Mulungu amaletsa kuchotsa moyo ndiye wina aziima pachulu nkumati ukapha ulubino ulemera? Nzeru zimenezi wazitengera kuti? Ine ndidayamba usinganga kalekale koma sindidalandireko chivumbulutso chimenecho. +Ndiye tiziti omwe amapha maalubinowo amapita nawo kuti? Choyamba zindikirani kuti anthu ena amangonamizira usinganga asali nkomwe ndiye anthu oterowo ndiwo amanamiza anthu omwe akuwaona kuti azingwitsitsa nkumawalamula kuti apereke ndalama zankhaninkhani. Ena ndi aja amanamiza ana asukulu kuti ali ndi mankhwala okhozetsa mayeso mapeto ake ana osawerenga kudalira mankhwalawo mapeto nkudzalakwa mayeso. +Koma mankhwala olemeretsa alipodi? Chilungamo nchakuti palibe mankhwala kapena chizimba cholemeretsa koma munthu akalimbikira ntchito nkulemera apa ndiye mankhwala otetezera chumacho amapezeka. Mundimvetsetse kuti uku kumangokhala kuteteza chuma osati kuonjezera chuma, ayi. +Nanga zikhulupiriro zina monga zija zoti munthu akagone ndi mayi ake kapena mwana wamngono kuti alemere nzoona? Ayinso, sizitheka. Kungoti asingangawo amakhala kuti adya ndalama zambiri za munthuyo ndiye amadziwa kuti mayi ake sangalole komanso akagona ndi mwana wamngono apalamula mlandu ndipo amangidwa kenako iye aziti munthuyo waphonya chizimba yekha, cholinga ndalamazo asabweze kwa mwiniyo. +Ndidamvako anthu akunena kuti ena adagona ndi amayi awo kuti apeze chuma, mukutanthauza kuti amenewo ankangobwebweta? Eee, ndipo sadziwaso chomwe akunena kapena kutanthauza. Mudzafufuze monga mwa ntchito yanuyi, mudzaona kuti singanga woteroyo akauza munthuyo zokachita ngati zimenezi amamuuzanso kuti azikalimbikira nthito yake kaya ndi ya kumunda kaya ndi bizinesi ndiye chuma chimachokera mukulimbikiramo, osati poti wagona ndi mayi ake. +Pali mawu ena mwina? Eya, mawu alipo kwa akuluakulu monga aboma ndi achitetezo kuti akhwimitse malamulo otetezera anthuwa chifukwa mapeto ake, zolakwa zopanga anthu ena, lidzaipa ndi dzina la asinganga. +Mwina awerengi ena akhoza kukhala ndi mafunso angakupezeni bwanji? Akhoza kundiimbira foni pa 0999 281 903 kapena 0888 890 957 kapenaso 0111 979 290 olo kungofika ku area 22 ku Lilongwe nkufunsa adzandipeza ndipo ndidzawayankha mafunso awo. +Zampira zenizeni ndi CJ Banda John CJ Banda ndi kaputeni wa Blue Eagles, komanso ndi katundu wofunika ku Flames. Iye wapeza mwayi wokasewera ku Jomo Cosmos mdziko la South Africa. Kodi apita liti? Nanga mbiri yake ndi yotani? BOBBY KABANGO akucheza naye. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Dzina lonse ndi ndani? Banda: Amanditcha CJ Dzina langa ndi John Banda koma ondikonda amati John CJ Banda. +Okukonda ake ati? Nanga CJ akutanthauzanji? Anthu a kwathu ku Nkhata Bay ndiwo adandipatsa dzina la CJ, chidule cha Christopher John Banda amene ankasewera mu Big Bullets. Ati timasewera mpira wofanana. Ena amaganiza kuti adali bambo anga koma ayi, padalibenso chibale ndi ine. +Tamva kuti ukupita ku South Africa, unyamuka liti? Ulendo mwina ulipo kapenanso ayi. Izi zili chonchi chifukwa eni akewo adamaliza nambala ya osewera akunja amene amayenera alembe komanso nkhani yeniyeni yomwe ndikudziwa ine ndi yakuti sadamalize kupereka ndalama kutimu yanga yomwe adagulira Micium Mhone. Koma zonse zikatheka ndiye mu May muno tipitako komanso dziwani kuti pali matimu ena amene akundifuna ngakhale matimuwo sindingawatchule maina awo pano. +Koma mayeso mudakhozadi? Kwambiri, ngakhale mutafunsa eni timu akuuzani kuti zidatheka, ntchito tidagwira. +Tandiuzako za chiyambi chako pa chikopa. +Ndidayamba kusewera mpira ku Eagle Strikers mu 2008. Tidali osewera amene tidailowetsa muligi ndipo idatha chaka osatuluka. Mu 2010 ndidachokako ulendo ku Police Training School. Kuchoka uko ndi pomwe ndimadzayamba kusewera mu Blue Eagles. Tidawina Standard Bank Cup mu 2011, Carlsberg Cup mu 2012 ndi Fama Cup mu 2012. +Nanga mbiri yako ku Flames? Ndidatengedwa kukasewerera Flames mu 2011 pamene timamenya ndi Kenya. Ndasewera magemu 46 ndipo ndachinya zigoli 10, chaka chathachi ndidachinya zigoli zinayi kuposa osewera aliyense mu Flames. Koma ndimasewera pakati. +Uli pabanja? Mkazi uyo akumvayo, dzina lake Jane komanso mwana alipo dzina lake Sean. +Kodi udindo wako ndi wotani ku polisiko? Ndine Inspector kulikulu la polisi ku Area 30. +Za mafumu mmatuni ndi mmizinda Kalata yangayi ndikulemba kubwereza zomwe nthawi ina patsamba lomwe lino ndidadandaulapo zokhudza maufumu a mmizinda ndi mmatauni. Lero ndabweranso kupempha boma kuti libwere poyera popanda kuzengereza kutiuza kuti maufumu alipo mmalokeshoni athuwa ndi mmapuloti kapena ayi zinthu zisanafike poipa. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mfumu ya mzinda wa Blantyre: Noel Chalamanda Monga mumzinda wa Blantyre muno, chomwe ndikudziwa ndi choti a Malawi Housing Corporation ndi omwe amagawa nyumba kapena mapuloti kwa amene apeza mwayi panthawiyo. Si mfumu imene imagawa nyumba kapena puloti. Lero lino kwabadwa mafumu amene akuika anthu mmalokeshoni ndi mmapuloti muukapolo. +A boma adziwe kuti mafumuwa akhazikitsa timalamulo tozunza komanso kuba monga kukalipira ndalama pamene mukukapereka uthenga wa maliro (mabanja a ku Chimwankhunda mumzinda wa Blantyre amalipira K3 000 ena mpaka K4 000 kwa mfumu Zingwangwa). Tangoganizani, ndi mabanja angati amene aferedwa ndipo akusowa kuti athandizidwe? Khansala wa derali akudziwa bwino za nkhani imeneyi. +Chomwe ndikudziwa ine ndi choti mfumu ya mzinda uno ndi Mayor ndipo amathandizidwa ndi makhansala amene timasankha mmawodi athu. Za mafumuzi ine sindikugwirizana nazo chifukwa cha kusokoneza. Mafumu kumudzi, osati mtauni muno. +Mudali mu Sitandede 1 Dzina la Julius Mithi si lachilendo. Ndi kadaulo pa zowerengetsa komanso wagwirapo ntchito kubungwe la zamasewero la FAM. Ngakhale ambiri angamudziwe mkuluyu, zambiri za banja lake sizidziwika komanso momwe adatumbira namwali wake. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mithi akuti naye ndi wosongoka pakamwa ndipo adatumba kale womusangalatsa. Uyu ndi Ella Msopa Kumwenda amene lero ndi mayi Mithi. +Mithi ndi mkazi wake Ella Ndi banja lachitsanzo, lonyadirana ndipo Mulungu sadalimane mphatso za ana awiri kuwonjezera chimwemwe chawo. Kodi nanga Mithi adamasuka bwanji pakamwa kuti athere mawu Ella? Chithokozo chipite kwa makolo a awiriwa potumiza ana awo ku Vongo FP School mboma Mzimba. Awiriwatu adaponyerana maso ali sitandede 1. +Kodi nthawi imeneyi Mithi adali atadziwa kale kusula Chichewa? Ayi, timangokondana mwachibwana. +Nanga Chichewa adasula pati? Ndinachoka ku Vongo kubwera ku Mzuzu mu 1981 kudzakhala ndi bambo anga ndipo panadutsa zaka 7 pomwe sitinathe kuonana, kufikira ine nditayamba ntchito mboma mu 1992. Apo Ella anali ku Ekwendeni Nursing School. Mwamwawi tinadzakumana ku Mzuzu pomwe chibwenzi chathu chidayambiranso. Atatha zaka 4 kusukulu ya unamwinoko tidakwatirana. +Mithi akuti zinthu izi zidamukoka kuti asadumphitse mawu pa wokondedwa wakeyu: Ndinamufunsira chifukwa adali mtsikana wofatsa komanso amachoka kwathu, kwawo ndi kwa agogo anga. +Okondanawa akuti panthawiyo adalibe ndalama zomangitsira ukwati ndipo adangodalitsa ku St Peters Cathedral Parish ku Mzuzu mu 2008. +Zidayambira mmalingaliro Mwina tinganene kuti kulimbikira ntchito ndiko kudapangitsa kuti malingaliro omwe Steve Chimenya wa ku Zomba adali nawo asanduke zenizeni ndi kubweretsa chimwemwe mmoyo mwake. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mnyamatayu akuti amati akakhala payekha, mmutu mwake munkabwera chithunzithunzi cha msungwana yemwe adali asadamuoneko nkale lonse kufikira mchaka cha 2014 pomwe tsiku lina kuofesi yake kudatulukira msungwana wofanana ndi wa mmalingaliro akewo. +Chimenya ndi nthiti yake patsiku laukwati wawo Rachel Jeremiah Sato wa ku Ntcheu yemwe akuti amagwira ntchito kunyumba ya boma adatumidwa kukagwira ntchito komwe Steve ankagwira ntchito ndipo uku nkomwe zonse zidayambira. +Nditamuona, ndidadzimenya mmutumu kuganiza kuti kapena malingaliro aja andipezanso nthawi ya ntchito. Kenako ndidamuona akulowa muofesi yanga ndipo ndidakhulupirira kuti sadali malingaliro chabe. Ndidamupatsa moni, iye nkuyankha, adatero Steve. +Iye akuti tsikulo adaweruka mosiyana ndi masiku onse moti olo anthu okumana naye tsikulo ankadabwa ndi nkhope yowala yomwe adali nayo. +Iye akuti chiyambi cha chikondi chawo chidali chomwecho mpaka pa 26 September 2015 adachita chinkhoswe kumudzi kwawo kwa Rachel ku Ntcheu ndipo pa 14 November 2015 lidali tsiku la ukwati woyera womwe madyerero ake adachitikira ku Capital Hotel ku Lilongwe. +Rachel akuti iye atangomuona Steve chinthu chidamugunda mumtima ndipo patapita masiku angapo pomwe Steve ankamuuza za chikondi, mumtima mwake adali atamukonda kale ngakhale kuti panthawi yomwe ankangocheza iye sankaonetsera. +Khama Khwiliro: Katakwe pa nyimbo zauzimu Khama Khwiliro ndi mmodzi mwa oimba nyimbo zauzimu amene ambiri otsata nyimbozi amamudziwa. CHIMWEMWE SEFASI adakumana naye ndipo adacheza motere: Ndikudziwe Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Dzina langa ndine Khama Khwiliro, ndidabadwa pa 15 April 1983. Kwathu ndi mmudzi mwa Mtengula, kwa T/A Chikowi ku Zomba. +Kodi udakwatira? Maso patsogolo: Khwiliro Khama ali pabanja ndipo adakwatira Jackina Meleka ndipo adadalitsidwa ndi mwana mmodzi, dzina lake Tawina. +Kodi zoimbaimba udayamba liti? Ndidayamba kuimba mma 1990. Koma mu 2010 mpamene ndidatulutsa chimbale changa choyamba chomwe mutu wake ndi Nthawi Yanga Yakwana. +Kodi uli ndi zimbale zingati? Inetu ndili ndi zimbale ziwiri: Nthawi Yanga Yakwana komanso Ndaona Kuwala. +Uthenga wako wagona pati nanga umaimba zamba zanji? Uthenga wagona pa za mawu a Mulungu okamba zoyenera kuchita monga Akhristu makamaka nthawi yotsiriza ino. Nyimbo zikulukidwa mu zamba monga manganje, kwaito ndi zamba zina za kwathu kuno. +Pambali poimba umagwiranso ntchito ina? Nanga umakonda chiyani ngati sukuimba? Inetu ndimagwira ntchito ku Blantyre Synod Health and Development Commission komanso ndikakhala kuti ndili ndi mpata, ndimakonda kucheza ndi anthu osiyanasiyana. Kumbali ya zakudya, ndimakonda nsima ya chisoso ndi chambo. +Kuimba umafuna utafika nako pati? Ndimafuna kuimba kutafika ngati mmene anzathu akunja amachitira komanso anthu azitha kukwanitsa kusamala mabanja awo kudzera mkuimba ndi kupeka nyimbo. +Asemphana pankhani ya malata, simenti sabuside Pali kusiyana Chichewa pandondomeko ya malata ndi simenti zotsika mtengo, pamene anthu omwe akuyenera kupindula ndi ndondomekoyi akuti boma tsopano likungopereka zipangizo zokha popanda ndalama zomangira nyumba monga momwe lidawalonjezera. +Koma mneneri wa unduna wa zamalo, Charles Vintulla, watsutsa zoti pali kusintha kulikonse ponena kuti boma lapereka kale zipangizo kuphatikizapo ndalama kwa anthu ovutika zoti amangire nyumba. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Iyi mdi imodzi mwa nyumba zomwe zamangidwa kupyolera mu pologalamu ya sabuside ya malata ndi simenti Ena mwa amene apindula ndi ndondomeko ya zipangizo zotsika mtengo zomangira nyumba auza Tamvani kuti boma lidawapatsa malata ndi simenti mu January chaka chino ndipo ati mu February adauzidwa kuti alandira ndalama zomangira nyumbazo. +Mpaka mwezi uno wa May boma akuti silidawapatsebe ndalamazo, zomwe zapangitsa kuti anthu ena ayambe kugulitsa zipangizozo komanso ena ayamba kumanga pogwiritsa ndalama zamthumba. +Elina Bamusi wa mmudzi mwa Gulupu Chalunda, kwa T/A Phambala, mboma la Ntcheu, ndi mmodzi mwa anthu amene ayamba kumanga nyumba pogwiritsira ntchito ndalama zawo. +Ndidalandira malata 30 komanso matumba a simenti 30. Nditalandira katunduyo, adati tidikire ndalama zomangira. Tadikira mpaka lero, kenaka akutiuza kuti timange ndi ndalama zathu. +Ndapeza anyamata amene akundimangira pamtengo wa K130 000. Achibale ndiwo andithandiza ndi ndalamayi komanso kwinako ndidapanga geni ya makala, adatero mayiyu. +Bamusi adati pamwamba pa malata ndi simenti adawauzidwa kuti boma liwapatsa K190 000 aliyense yomangira nyumba. +Adatiuza kuti ndalama yonse yomangira nyumba ndi K380 000 koma adati ife tidzabweza K190 000, boma lidzaikaponso K190 000 koma tikudabwa kuti izi sizidachitike ndipo angotipatsa zida popanda ndalama, adatero mayiyu. +Anthu ena atatu amene sadafune tiwatchule maina, adati chifukwa cha kusintha kwa ndondomekoyi, iwo agulutsa zipangizo zomwe adalandira kuchokera kuboma. +Ndinalandira malata 30 ndi matumba 30 a simenti ndipo ndimadikirira ndalama zomangira nyumba koma mpaka lero kuli zii. Ndangogulitsa matumbawo moti angotsala asanu ndi malata 20, adatero mkuluyo. +Koma izi zikudabwitsa Vintulla, yemwe wati zomwe akukamba anthunzi ndi zosiyana ndi mgwirizano womwe boma lidapanga ndi iwo. +Ndi zoona kuti akalandira zipangizo, boma lizipereka ndalama yomangira nyumba. Ndalama yake ndi K50 000, osati K190 000, monga akukambira ndipo ndalamayi tidatumiza kale mmaboma awo, adatero Vintulla. +Munthu aliyense akumayangana yekha womanga, ife tikumangopereka K50 000 yoti amangire. Ngati womangayo wawatchaja ndalama zambiri, ife tidzaperekabe K50 000, adaonjezera Vintulla. +Pokambapo pa za anthu ena amene akugulitsa zipangizo zawo, iye adati palibe chosintha, anthuwo adzaperekabe gawo lawo kuboma ngakhale katunduyo wagulitsidwa. +Ndondomekoyi ndi yothandiza anthu ovutikitsitsa, iwo ndi boma aliyense akuperekapo theka kuti nyumba imangidwe. Ngati agulitsa zipangizo, adzaperekabe mbali yawo, adatero. +DC wa boma la Ntcheu, Harry Phiri adati akuyenera afufuze kaye ngatidi alandira ndalamazo. Paja ndili paulendo wopita ku Phalombe, ndiye ndikuyenera ndifufuze kaye, adatero. +DC wa boma la Nkhata Bay, Alex Mdooka adati kumeneko alandira ndalamazo Lolemba lathali. +Tangolandira kumene Lolembali, koma zipangizo ndiye zidafika kale. Apa ndiye kuti anthu akuyenera apatsidwe ndalamazi kuti ayambe kugwiritsa ntchito, adatero. +T/A Nkhulambe wa ku Phalombe akuti kumeneko palibe chachitika ngakhale madera ena anthu ayamba kusangalala ndi ndondomekoyi. +Maina adalemba kalekale, koma mpaka lero palibe walandirapo malata kapena simenti. Sitikudziwa kuti vuto nchiyani. Anzathu ku Mulanje adalandira kalekale koma kunoko palibe chikuchitika, adatero. +Chimodzimodzi Senior Chief Kanduku ku Mwanza akuti nakonso ndalama zoti anthu amangire nyumba sizidafike kumeneko koma zipangizo zokha. +Ndondomeko yopereka zipangizoyi ikuyembekezeka kupindulira anthu 80 mdera la phungu aliyense wa Nyumba ya Malamulo. +Anatchezera Ndazunguzika Agogo, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndine mtsikana wa zaka 18 ndipo ndinazunguzika mutu chaka chatha pomwe ndinapezeka ndi kachilombo ka HIVkoma sindinagonepo ndi munthu ngakhale ndinali nacho chibwenzi. Amayi anga ali ndi HIV koma abambo anga alibe. Banja la makolo anga lidatha ndili ndi chaka ndi miyezi isanu ndi iwiri. Ine ndine woyamba kubadwa koma ana onse obadwa kwa amayi anga amabadwa ndi kachilombo. Amayi anga akuti adatenganso pathupi ine ndili ndi miyezi 9 koma abambo anga amakana kuti mwanayo adali wawo. Ndiye ine zinandizunguza mutu kuti kodi zidayenda bwanji. Abambo anga ndi amayi anga ondipeza amandinena kuti ndinatenga kachilomboka kwa chibwenzi chomwe ndinali nacho. Mankhwala ndinayamba kumwa sabata yomwe anandipeza ndi kachilomboka popeza chitetezo chinali chotsika kwambiri, koma sindinadwale, ndidangopita ndekhala kukayezetsa ndipo ndinalibe nkhawa iliyonse. Koma pano ndikusowa mtendere. Ndithandizeni, chonde, nditani? RM, Mzuzu Zikomo RM, Nkhani yako ndaimva bwino lomwe ndipo ndakunyadira chifukwa ndiwe mtsikana wolimba mtima. Si ambiri amene amalimba mtima kukayezetsa magazi ngakhale sakudwala kuti adziwe momwe chitetezi chilili mthupi mwawo, ambiri amaopera kutalitali-safuna kudziwa nkomwe ngali ali ndi kachilombo kapena ayi. Wanena kuti udapezeka nndi kachilombo ka HIV chaka chatha koma wanenetsa kuti sudagonanepo ndi munthu wina aliyense ndiye zidatheka bwanji kupezeka ndi kachilomboka? Iyidi ndi nkhani yozunguza chifukwa ngakhale pali njira zambiri zotengera kachilomboka, njira yodziwika kwambiri ndi yogonana ndi munthu amene ali nako mosadziteteza. Koma zimatheka ndithu kutenga kachilomboka mwatsoka ndithu ndipo imodzi mwa njira zotere ndi kutengera kachilomboka pobadwa kuchokera kwa mayi amene ali nako. Ndikhulupirira iweyo udatenga kachilomboka panthawi yobadwa chifukwa wanena kuti ana onse obadwa mwa mayi ako akumapezeka ndi kachilombo ka HIV. Chomwe ndingakulangize nchoti pitiriza kumwa mankhwala otalikitsa moyo ndipo udzisunge monga wadzisungira nthawi yonseyi ndipo udzakhala ndi moyo wautali, wosadwaladwala. Uziyesetsa kuti usamakhale ndi nkhawa chifukwa izi zikhoza kubweretsa mavuto ena pamoyo wako. Uzilandira uphungu woyenera kwa akatswiri odziwa za kachilombo ka HIV kuti ukhalebe ndi moyo wathanzi ndi wansangala, osati kudzimvera chisoni. Kupezeka ndi kachilombo sikutanthauza kuti ufa nthawi iliyonse, ayi, utha kukhala zakazaka mpaka kukalamba monga ine, bola kudzisamalira. +Amadikira ndimuimbire Anatchereza, Ndine mtsikana wa zaka 15 ndipo ndili ndi chibwenzi koma anapita ku Nkhotakota. Poyamba timaimbirana foni koma panopa adaleka, amadikira ine ndiimbe. Kodi pamenepa ndimudikire? Agogo, ndithandizeni. +TG Mtakataka Zikomo TG, Kunena zoona mwana iwe wafulumiza kukhala ndi chibwenzi. Za sukulu uli nazo pafupi iwe? Ndakaika. Iwe, mwana wa zaka 15, chibwenzi nchachiyani, mwanawe? Ayi ndithu, ukayamba zibwenzi pamsinkhu wakowo sizidzakuthera bwino kutsogolo ndipo udzanongoneza bondo. Mwana wamngono ngati iwe sayenera kukhala ndi zibwenzi koma kuika mtima pamaphunziro chifukwa sukulu ndi yofunika kwambiri. Sunandiuze kuti bwenzi lakolo lili ndi zaka zingati, koma ngati ndi munthu wamkulu ndikhulupirira wazindikira kuti si bwino kukhala pachibwenzi ndi mwana wamngono ngati iwe, nchifukwa chake sakulabadira zokuimbira. Ndiye ngati umamva, chonde musiye ndipo uike mtima pasukulu! Ukapanda kumva langizo langa, kaya zako izo! Usadzati sindinakuuze. +Kumaona pomvetsera mahedifoni Malinga ndi kusintha kwa zipangizo zogwiritsa ntchito, moyo ndi makhalidwe a anthu zikunka zisintha tsiku ndi tsiku. +Pafupifupi aliyense ali ndi foni yammanja ndipo achinyamata ambiri ali ndi zida zanyimbo zomwe akamayenda amakhala akumvetsera pogwiritsa ntchito mahedifoni. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kumvetsera nyimbo si chithu cholakwika, kungoti nthawi zina kagwiritsidwe ntchito ka mahedifoni timakhala ngati sitimakaganizira bwino, makamaka tikakhala pamsewu. +Masiku ano umapeza munthu akuyendetsa njinga pakati pa msewu mahedifoni ali kukhutu kotero kuti kaya diraiva wa galimoto aimbe bwanji hutala, wapanjinga samva chifukwa cha nyimbo zomwe akumvetsera. +Madiraiva enanso a minibasi ndi galimoto zina amagundika kukweza nyimbo za mahedifoni ali pamsewu osaganizira kuti akusokoneza ntchito yomwe makutu amayenera kugwira posamala kayendedwe ka pamsewu. +Aliponso ena oyenda pansi omwe akalonga mahedifoni mmutu amangodziyendera pamsewu mwamgwazo. +Choncho amapezeka kuti akuyenda pakati pa msewu kapena kuoloka nthawi yolakwikwa chonsecho makutu atseka ndipo sakumva chilichonse chochitika pamsewupo. +Khutu ndi chimodzi mwa ziwalo zomwe oyendetsa galimoto komanso oyenda pansi amayenera kugwiritsa ntchito pamsewu kuti amvane, komanso kupewa ngozi ndiye zingathandize kuti azipatsidwa mpata. +Ndi zinthu ngati zimenezi munthu susungulumwa kwenikweni, koma kupanda kusamala nazo zingathe kuchititsa ngozi zomwe zikadatha kupeweka. +Pamsewu pamachitika zinthu zambiri ndipo pamakhala anthu osiyanasiyana-ena amgwazo, ena achangu, ena oledzera. Choncho nkofunika kuti ukamayendapo nzeru zonse zizikhala pamsewupo mmalo momamvera nyimbo utasiyira ena kuti akusamalire moyo wako. +Matimu 8 mu Presidential Cup Wolemba BOBBY KABANGO M atimu 8 ndiwo atsala kuti aswane mndime ya makotafainolo a mpikisano wa Presidential Cup kutsatira kupambana kwa Nyasa Big Bullets yomwe imathirana wonga ndi Blue Eagles Lachitatu lapitali pabwalo la Nankhaka mumzinda wa Lilongwe. +Awa ndiwo adali masewero omaliza kuti apeze timu ya nambala 8 kutsatira kuchita bwino kwa matimu ena. +Matimu a Mighty Be Forward Wanderers, Moyale, Kabwafu, Epac, Mafco, Dwangwa ndi Max Bullets ndiwo adafika kale mndimeyi atachita bwino pamasewero awo. +Nkhondo yolimbirana malo mundimeyi pakati pa apolisi a ku Lilongwe ndi timu ya fuko yak u Blantyre idali ya mtima bii komanso adali masewero ochititsa kaso chifukwa matimu awiriwa ndiwo akhala akuchita bwino mmasewero awo muligi ya TNM. +Matimuwa adalepherana patatha mphindi 90 ndipo woimbira Mabvuto Msimuko adaloza malo aimfa kuti atulutsane kudzera mmapenate. +Bashir Maunde, Muhammad Sulumba, Chiukepo Msowoya, Yamikani Fodya ndi Pilirani Zonda ndiwo adachinyira Bullets. Mike Mkwate, John Lanjesi ndi McFallen Ngwira a Bullets adaphonya mapenate awo. +Eagles idachinya kudzera mwa Osward Maonga, Gregory Latipo, Victor Nyirenda ndi Gilbert Chirwa, pamene Winster Phiri, John Malidadi, Ackim Kazombo ndi Enock Likoswe adaphonya. +Dolo wa tsikuli adali goloboyi wa Bullets, Ernest Kakhobwe, yemwe adagwira mapenate atatu a Eagles kuphatikizapo yomaliza yomwe adasewera Likoswe, kupangitsa kuti Bullets ifike mndime ya makotafainolo. +Lero Dwangwa ilandira Mafco pa Chitowe pamene Epac ituwitsana ndi Moyale pa Civo Stadium. +Tsiku limene Max Bullets iphulitsana ndi Wanderers komanso limene Bullets iphulitsane ndi Kabwafu pakwawo alengezabe mtsogolo muno. +Adzikhweza pamkangano wa madzi osamba ku Nkhatabay Chisoni chakuta banja lina ku Bula, T/A Mbwana, mboma la Nkhata Bay pomwe mnyamata wa Sitandade 8 wadzimangirira atayambana ndi mlongo wake. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Malinga ndi mfumu Dumbulira ya derali, Chrispin Mwale adayambana ndi mlongo wake pankhani ya madzi osamba. +Mfumuyi idati chifukwa cha ichi mnyamatayo adadzimbuka ndi kupita kutchire. +Abambo ake adamutsatira kutchire konko koma adadzawathawanso nkubwererako. Adafikira kuchipinda chake chogona, idatero mfumuyo. +Malinga ndi mfumuyo, mayi a mnyamatayo adadabwa pomwe adatuma mwana wina kukatenga chinangwa choti aphike ndipo mwanayo adapeza mbale wakeyo atadzimangirira ndi chitenje. +Koma pambalipa adasiya kalata yomwe adalembera mphunzitsi wamkulu wa pasukulu ya pulaimale ya Munthelele yowatsanzika kuti sapitiriza sukulu chifukwa moyo wake watha, Dumbulira adatero. +Iye adati kudzikhweza kukukula mderalo koma samayembekezera kuti mwanayo angalimbe mtima motere chifukwa adali wanzeru komanso wolimbikira pa maphunziro. +Naye mneneri wa polisi mboma la Nkhata Bay Ignatius Esau adatsimikiza za imfayo. +Ndi zoona kuti mwana wa zaka 15 wadzikhweza ku Bula ndipo nawo achipatala atsimikiza kuti adadzipha kaamba kodzimangirira, adatero Esau. +Amanga wometa mnzake kumanyazi Zachilendo akuti zachitika ku Mangochi komwe apolisi amanga mkulu wina pomuganizira kuti adameta mnyamata wa fomu 4 malo aulemu. +Mneneri wa polisi ya Mangochi Rodrick Maida watsimikiza za kumangidwa kwa Kenneth Chimombo, wa mmudzi mwa Mtalimanja, kwa T/A Mponda mbomalo. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Maida wati apolisi amutulutsa mkuluyu pabelo pamene kufufuza zenizeni za nkhaniyi kukupitira. Iye akuti amutsekulira mlandu wogwira munthu malo osayenerera (indecent assault). +Maida adati Chimombo adakumana ndi mnyamatayo Lachitatu pa 23 March pomwe adagwirizana kuti akachezerane. +Mnyamatayo adauza apolisi kuti wakhala nthawi asakupita kunyumba kwa Chimombo ndipo patsikulo atakumana, Chimombo adamuuza kuti abwere kunyumba kwake kuti akacheze, adatero Maida. +Cha mma 10 koloko mmawa wa tsikulo, mnyamatayo, amene ali ndi zaka 18, akuti adapita kunyumbako ndipo adamupeza Chimombo ndi mwana wina kunyumbako. +Maida adati mnyamatayu wauza apolisi kuti adauzidwa ndi Chimombo kuti apite kuchipinda komwe ati kudachitika zoda mutuzi. +Akuti panthawi yomwe amauzidwa izi, thupi lake lidafooka, zomwe zidamuchititsa kuti achite chilichonse chomwe amalamulidwa. +Kuchipindako akuti adayamba kumusisita pamimba ndipo adayamba kumumeta pamimba. Akuti panthawiyi adafooka ngati wabaidwa jakisoni wa dzanzi. Akumumeta choncho akuti adadzidzimuka pamene Chimombo adayamba kumugwira malo obisika kuti amumete, adatero Maida. +Apa akuti ndi pamene adazindikira ndipo adatuluka mnyumbamo ulendo kukanena kwa makolo ake. Panthawiyo akuti adayamba kusanza ndipo adafooka kwambiri. +Makolo a mnyamatayu akuti ndiwo adapita ndi mwana wawo kupolisi ya Mangochi kukadandaula kuti awametera mwana wawo. +Kupolisi adavula kuti tione, ndipo tidaonadi kuti adali wometedwa. Ndiye tidamanga Chimombo tsiku lomwelo pomuganizira kuti wachita izi ndi iye chifukwa ndiyenso amatchulidwa, adatero. +Koma Chimombo, wa zaka 29, akuti wauza apolisi kuti adametadi ndi iyeyo pamene adauzidwa ndi mnyamatayu kuti amumete. +Sadakane kupolisi, iye wati adachita kutumidwa ndi mnyamatayu kuti amumete. Tidamutengeranso kubwalo la milandu komwe amakauzidwa za mlandu womwe akuzengedwa, adaonjeza Maida. +Ngati Chimombo akapezeke wolakwa pamlanduwu, atha kukakhala kundende zaka zitatu, malinga ndi malamulo a dziko lino. +Aphungu avuta Tsikulo pa Wenela padali ziii! Moti ojiya, osolola ndi osenza onse adali khumakhuma. Ndalamatu, ndalama zalowa ku silent ndiye anthu sakuyenda. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Basi ya Lilongwe imatenga tsiku lonse kuti idzadze. Ambirinso amachita kunenerera. Nchifukwa chake ndidangoganiza zolowera malo aja timakonda pa Wenela. +Ndidakapeza Abiti Patuma ndi Gervazzio akumvera nyimbo ya Lucius. +Poti sitima, imaphweka akamayendetsa wina. +Sindikudziwa kuti nyimboyo adaika chifukwa chiyani! Abiti Patuma adali bize pafoni yake. +Koma abale, phungu uyunso ndiye amangokhalira pa Facebook. Taonani lero akuti iye sakufuna kukwezeredwa ndalama. Ndidakuuzani kale kuti uyu wokonda kuvina kanindoyu amangofuna kuti anthu azimumvera. +Mwaiwala zija ankanena zolodza azungu osakaza la Mulanje phiri; mwamuiwala kuti ngwanthabwala basi? adatero Abiti Patuma. +Zoona. Chomwe ndikudabwa nchakuti kodi bwanji phunguyu akutokota pa Facebook mmalo mwa pagulu la aphungu anzake? Ndikuona ngati nzeru zikumuchepera kapena Chingerezi ndiye vuto kwa regisrator (sic) ameneyu, adayankhira Gervazzio. +Abale anzanga, kunena zoona wamisala adaona nkhondo. Vuto limakhala lakuti iye sadathawe, adakhala limodzi ndi anthu ena mmudzimo. Iyetu adafera limodzi ndi ena onse. +Kodi iyeyo ngakhale akulankhula pa Facebook kuti anthu amutamandire, malipiro atakwezedwa iyeyo angakane? Chiphimbammaso ichi basi, ndidailowerera. +Koma zonse zili apo, aphunguwa akutionjeza pano pa Wenela. Ndalamatu zalowa ku silent ndiye wina azifuna mamiliyoni pamwamba pa mamiliyoni anzake. +Ndiye ndinamva wina akunena kuti amalandira zosaposa K250 000. Bodza inu! Momwe anthu awa amayendera, kumalandira maalawansi ochuluka aziti akulandira zochepa? Anthu awa Mulungu adzachititse nthaka iwameze tsiku lina, adatero Abiti Patuma. +Usiku wa tsikulo ndidalota maloto odabwitsa. Ndidalota nditapita ku Nyumba ya Malamulo ngati mlendo wa phungu wathu pa Wenela, Mr Water Bouncer, mzungu wathu. +Kutuloko ndidaona kuti nyumbayo idapita patsogolo kwambiri. Adali kulankhula ndi phungu wina amene adakhalapo msirikali woimba mabatcha. +Indetu ndinena ndi inu aphungu anzanga. Dziko lafika pena. Tatukuka. Onani tili ndi ma tablet, ma laptop, mafoni a touch ndi zida zina koma tikulephera kuzigwiritsa bwino ntchito. Kulibe Wi-fi, adali kutero mkulu wathupi lakeyo. +Musandifunse kuti Wi-fi nchiyani chifukwa sindingakuuzeni. Nanga ndichite kukuuzani kuti ndi njira imene anthu angalumikizire makina ndi mafoni awo ku Internet popanda chingwe? Ndimayesatu tsitsi la mbuu ndi mgodi wa nzeru, koma apa zikuoneka ndi zina. Mukalandira ndalama zankhaninkhani tsono mukufunanso Internet yaulere? Mmalo moti mumenyere ufulu kuti Internet ikhale yaulere kwa ana asukulu! Mubwereratu koimba mabatcha kuusirikali, adamuyankha phungu wina. +Ndidadzidzimuka. +Tidacheza nawo bwanji? Mchaka cha 2015 tamva zikhulupiriro, miyambo komanso mbiri zosiyanasiyana za maderanso osiyana. Lero BOBBY KABANGO akutibweretsera macheza ochepa amene nkhani yake idatekesa anthu. +Afisi ogulitsa ku Dedza Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Nkhani iyi idadzidzimutsa anthu ambiri kumva kuti pali bambo wina amene akugulitsa afisi. Iye adati fisi wamkazi ndiye amadula pamtengo wa K9 000 ati chifukwa akakuswera pamene wamphongo amapanga K8 000. +Mkuluyu ndi Njale Biweyo wa mmudzi mwa Masakaniza kwa T/A Kaphuka mboma la Dedza. +Biweyo adati ntchito ya afisiwo ndi kuteteza usiku, kusakira nyama komanso kukwera ngati muli paulendo. Adati fisi ndi ndege yapansi yomwe imathamanga kwambiri. +Pamene timacheza naye, mkuluyu nkuti ali ndi afisi awiri koma adati ena adawagulitsanso chifukwa adali nawo asanu. +Iye adati adayamba mu 1965 kuweta afisi. Iye ntchito yake akuti ndi ya ulonda ndipo kudzera mtchitoyi, adapeza nawo afisiwa amene amamuthandiza pantchito yake. Komwe kukukhala mkuluyu adatilozera ampingo wina womwenso ukutetezeka ndi fisi wamkazi. +Dzina la Kachindamoto lidabwera bwanji? Chaka chimenechi tidacheza ndi Senior Chief Kachindamoto wa mboma la Dedza amene adatifotokozera momwe dzina lake lidabwerera. +Mfumuyi idati Chidyaonga ankamenya nkhondo kwambiri ndipo sankaopa. Azungu amene ankamenya nawo nkhondoyo adagonja ndi Chidyaonga. Anthu poona momwe mkuluyu akumenyera nkhondo adangomutcha dzina la Chidyaonga. +Mfuti kuti itulutse chipolpolo mukaomba nchifukwa cha wonga umene ukayaka umaphulika kuti phuu! Ndiye chifukwa ankalimbana ndi zimenezi, anthu adangoti Chidyaonga, kutanthauza kuti akumadya wonga wa mfuti. +Kachindamoto nayenso sankaopa nkhondo. Iyeyu sankaopa ngakhale zitavuta maka ngakhalenso moto umene amapanga nawo mwakutimwakuti monga mukumvera dzinalo. +Wotentha thupi sayandikira ngombe Mkazi amene thupi lake ndi la moto akuti sayenera kuyandikira ngombe kapena khola lake kuopetsa kuzibalalitsa chifukwa thupi lake ndi la moto. Izi ndimalinga ndi zikhulupiriro za Angoni ena achigawo chapakati koma kumva kwa ena kuchigawo cha kumpoto kwa dziko lino akuti mkazi sayandikira ngombe kuopetsa kuti asulutsa zizimba pakholalo. +Tidacheza ndi nyakwawa Chimpeni ya kwa T/A Phambala mboma la Ntcheu. Iye adati thupi la mayi amene adathera msinkhu ndipo wayamba kukhala kumwezi limakhala loopsa ku ngombe. +Iye adati mayi ameneyu saloledwa kuti adutse pakati pa ngombe zija zikamayenda kapena zikamawetedwa. Salolanso kuti alowe mkhola lake. Sangazikuse, sangakame kapena kutsekera pakhomo. Sangalowe mkhola ngakhale kukachotsa ndowe. +Nyakwawayi idati imakhulupirira kuti ngombezo zimabalalika ndipo zimayamba kugona mthengo. +Kusakatula malongedwe a ufumu wa Chitumbuka Apa tidacheza ndi nyakwawa Chibochaphere, ku Nkhamanga Kingdom mboma la Rumphi atangolongedwa ufumu. +Iye adati polonga ufumu wa Chitumbuka, pamakhala timiyambo tina tomwe wolongedwa ufumu ayenera kutsata. Choyamba, dzina likadziwika la amene alowe ufumu, dzinalo limayenera lipite kwa Sawira Chikulamayembe kuti akalivomereze. Monga mwamwambo, kwa Sawira supita chimanjamanja koma kukwapatira kangachepe mmanja. Kumeneko timati kuluvya pa Chitumbuka. +Afuna chitukuko chofanana mmadera a aphungu Ntchito za chitukuko mmadera oyimiriridwa ndi aphungu a ku Nyumba ya Malamulo chiyamba kufanana tsopano ntchito yodulanso malire ikachitika. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Bungwe loyanganira zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lati ntchitoyi tsopano ikungodikira katswiri wochokera kunja yemwe adzaigwire. +Zonse zatheka tsopano tikungodikira katswiri yemwe achokere kunja kudzagwira ntchito yodulanso malirewa. Katswiriyu sitikumudziwa koma atumizidwa ndi akuluakulu a bungwe la Commonwealth, chidatero chikalata chomwe bungweli lidatulutsa. +Mneneri wa bungwe la sisankho mdziko muno, Sangwani Mwafulirwa, adati kudulanso malirewa kuthandiza kuti aphungu onse 193 azikhala ndi madera ofanana komanso chiwerengero chofanana cha anthu. +Madera ena pakalipano ndi aakulu kwambiri pomwe ena ndi aangono kwambiri ndiye poti aphungu amagwira ntchito imodzi, tikufuna kuti madera awo akhale ofanana kuti ntchito ikhalenso chimodzimodzi, adatero Mwafulirwa. +Iye adati mwachitsanzo dera la chigawo cha pakati mboma la Lilongwe ndicho chili chachikulu kwambiri ndi anthu oponya voti 126 115 pomwe dera la chilumba cha Likoma ndicho chochepetsetsa ndi anthu ovota 6 933 basi. +Ngakhale pali kusiyana kotereku ndalama za chitukuko zomwe aphungu amalandira zotukulira madera awo zimakhala chimodzimodzi kutanthauza kuti ndalama zomwezo kwina zikuthandiza anthu ochuluka kuposa kwina. +Ngakhale zinthu zili choncho, palinso nkhani yosintha ndondomeko ya kayendetsedwe ka chisankho yomwe kauniuni wa malamulo akale adachitika ndipo komiti yomwe imachita kauniuniyu idatulutsa kale zotsatira zake. +Imodzi mwa mfundo zikuluzikulu mndondomeko yatsopanoyi ndi yakuti aphungu asamakhale ndi malire koma kuti boma lililonse lizikhala ndi chiwerengero cha aphungu potengera chiwerengero cha anthu mbomalo. +Mwafulirwa adati bungwe la MEC silinganenepo kanthu pa za tsogolo la ntchito yodulanso madera a aphungu potengera malamulo atsopanowa pokhapokha nthambi ya zamalamulo idzanene mfundo yomaliza. +Nzoonadi, ndondomeko yatsopanoyi idapangidwa koma sidaperekedwe kunthambi ya zamalamulo (Law Commission). Zonse zidzidziwika nthambiyi ikadzanena maganizo ake. Panopa tiyeni tibatsata zomwe zilipo, adatero Mwafulirwa. +Apolisi anjata wolemba ntchito apolisi Pamene Patrick Mayeso Nkhoma wa zaka 28 ndi anzake ena 35 amanyadira kuti ayamba kuzinyambita ndalama za boma akalembedwa ntchito yaupolisi, iwo sadadziwe kuti owalemba ntchitowo, adangofuna kuwatafunira ma K9 500 awo powanamiza kuti. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Malinga ndi mneneri wa polisi ku Machinga Davie Sulumba, apolisi a mbomali agwira Ellard Sanudi, wa zaka 32, pomuganizira kuti iye ndi mnzake wina amene pakadalipano sakudziwika komwe ali, adanamiza anthu kuti awalemba ntchito yaupolisi, zomwe zikutsutsana ndi ndi gawo 361 la milandu ndi zilango zake (Penal Code) la malamulo oyendetsera dziko lino. +Sulumba adati Sanudi ndi mnzakeyo akuwaganizira kuti adauza anthuwo kuti apereke maina awo, masatifiketi ndi nambala za foni komanso alipire K9 500 aliyense ngati atsimikizadi kuti akufuna kulembedwa ntchito kupolisi. +Anthuwa adalipiradi ndalamazi, ena pamanja pamene ena adalipira kudzera pa TNM Mpamba komanso Airtel Money, ndipo adawatsimikizira kuti pa 30 May chaka chino akakumane pabwalo la T/A Nsanama ku Machingako kuti akanyamuke pagalimoto ya polisi kupita kusukulu yophunzira ntchito zaupolisi, adatero Sulumba. +Tsikuli litafika anthu ofuna ntchitowa adafika pabwalo la mfumulo mwamachawi atanyamula zikwama zawo, koma kudangoti zii ngati kumanda, Sanudi ndi mnzake osatulukira pamalopo. Izi zidachititsa anthuwa kukamangala kupolisi. +Pakadalipano apolisi anjata Sanudi amene akuti adali ngati kalaliki wa oganiziridwawa, pamene mnzake, amene akuti adavala yunifomu ya polisi, akusakidwabe. +Kudzula: Mpeni wofunikira kwa butchala Popha mbuzi kapena ngombe amagwiritsa ntchito zida zosiyanasiyana monga nkhwangwa, zikwanje ndi mipeni. Umodzi mwa mipeniyi umatchedwa kudzula ndipo eni ake akuti mpeniwu amagwiritsa ntchito posenda nyamayo. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Innocent Chimsewu yemwe amapha nkugulitsa nyama ya mbuzi kuti adziwe chinsinsi chosagwiritsa mpeniwu pantchito zina koma kuphera ndi kusendera nyama basi. Iwo adacheza motere: Tandiuze dzina lako ndi ntchito yomwe umapanga, mnyamata. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Dzina langa ndine Innocent Chimsewu ndipo ndimapha mbuzi ndi kumagulitsa nyama yake mumsika wa ku Area 22A ku Lilongwe. +Kodi pali zinsinsi zilizonse zokhudzana ndi bizinesi ya nyama makamaka ya mbuzi kapena ngombe? Chimsewu kusenda mbuzi ndi mpeni wa kudzula Ndikudziwa zomwe mukutanthauza ngakhale mukukhala ngati mukukuluwika pangono ndipo yankho lake ndi ili: bizinesi ya nyama ya mbuzi kapena ngombe nchimodzimodzi bizinesi ina iliyonse. Apa ndikutanthauza kuti momwe anthu amayendetsera bizinesi ina iliyonse, ndimoso zimachitikira mbizinesi ya nyama. +Ndidamvako kuti mpeni wosendera nyama ya malonda sugwiritsidwa ntchito zina, zimenezi nzoona? Nzoona, mpeni umenewu tikamaliza kusendera mbuzi kapena ngombe timautsuka bwinobwino kuusunga pamalo abwino kuti usamalike. Kunena zoona si kuti pali kugwirizana kulikonse koma kuti anthu amangochita izi ngati njira imodzi yosamalira mpeniwu kuti usasowe. +Dzina la kudzula lidabwera bwanji? Ndi dzina basi monga momwe maina ena onse amayambira kapena kubwerera. Ena adangoganiza kuti mpeniwo ukhale kudzula mwina potengera ntchito yomwe umagwira yosendera nyama. +Umakhala mpeni wooneka bwanji? Ndi mpeni monga momwe umakhalira mpeni wina uliwonse koma uwu umakhala wakuthwa kwambiri komanso kawirikawiri, umaninga mmphepete imodzi ngati wosokera nsapato kaamba konolanola. Timanola pafupipafupi chifukwa mpeni wobuntha umanyotsola nyama posenda. Mnofu wambiri umatsalira kuchikopa. +Ndikubwezere mmbuyo pangono. Mpeni wa kudzula utasowa, mpeni wina uliwonse sungagwire nthito yosendera mbuzi kapena ngombe? Ukhoza kusendera bwinobwino popanda choletsa. Komansotu posenda mbuzi kapena ngombe si kuti pamakhala mpeni umodzi wokha, ayi, kungoti si mipeni yonse yomwe ili kudzula, koma wokhawo womwe ndalongosola uja ndipo umenewu ndiwo suloledwa kugwiritsa ntchito ina iliyonse Ntchito ina ya kudzula ndi chiyani? Kudzula amagwira ntchito zambiri pakupha ndi kusenda mbuzi ndi ngombe. Ntchito yoyambirira ndi yothyolera fupa la pakholingo. Wocheka pakhosi akacheka, pamakhala fupa lomwe limatsalira lomwe limasunga moyo ndiye amatenga kudzula nkuthyolera fupa limeneli. Ntchito ina, poti mpeniwu umakhala wakuthwa kwambiri, ndi kuchekera zammimba monga mtima, chifu, matumbo ndi ndulu. Makamaka pa ndulupo, ukagwiritsa ntchito mpeni wobuntha, mwangozi ukhoza kuthudzula ndulu ndiyetu kungotero, ndiwo yonse yaonongeka. +Nanga mubutchala mogulitsira nyamayo kudzula safunika? Si kwenikweni, iye kwake nkophera ndi kusenda koma zikavutitsitsa akhoza kugwira ntchito yochekera mubutchala si kuti china chake chingachitike, ayi, koma kuti ambiri amaumira kutero kuopa kusowetsa. +Wonyozedwa ali moyo Alemekezedwa atamwalira Gogo wina ku Ntcheu, yemwe amagona pachisakasa chonga pogulitsira tomato abale ake akukana kuti agone mnyumba yabwino, adalemekezedwa atamwalira ndipo siwa idali nyumba ya makono ya mmodzi mwa abale amamukana ali moyowo. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Batameyu James, wa zaka 67 wakhala akugona panjapo, samapatsidwa chakudya, amangodzionongera, ndipo mvula idakhala ikumuthera pathupi abale ake atatemetsa nkhwangwa pamwala kuti sangayerekeze kumuthandiza. +James mchisakasa chomwe ankagona Gogoyu asadamwalire, adauza Msangulutso pa 25 December 2015 kuti ankagwira ntchito yaulonda ku Lirangwe mboma la Blantyre koma pamene adabwerera kumudzi kwawo anthu sadamulandire. +Ndinkagwira ntchito yolondera. Ndidapita kale ndipo sindingakumbuke kuti ndi liti. Mkazi wanga adamwalira komweko, ndipo ndidaganiza zobwerera kumudzi kuno komanso nthawi yomwe ndimabwera nkuti ndikudwala, adatero gogoyu nthawiyo. +Koma ganizo lobwerera kumudzi kwawo kwa Howa, T/A Phambala silidakomere mchemwali wa gogoyu, Felisita James. +Gogoyo adafikira pamtengo, amagona pomwepo ndipo sabata isadathe akuti matenda adakula ndipo samayenda. +Chimbudzi ndikupangira pomwepa chifukwa sindingakwanitse kupita kuthengo. Miyendo yafa komanso ndikuzizidwa kwambiri chifukwa zofundazinso zikumanyowa kukabwera mvula, adatero akali moyo. +Titamufunsa Felesita chomwe sadamulandirire mbale wake, iye adati sakufuna kulankhula zambiri. Koma titamupempha kuti amulole gogoyu azigona mnyumba mwake, iye adati: Ngati alowe mnyumbamu ndiye ine ndituluka. +Kodi pali chifukwa chiyani chomwe akulangira mbale wawo? Muwafunse kuti adachoka liti pakhomo pano. Ndiye andifune lero? nanensotu ndine wokalamba chifukwa iwowo ndi ine wamkulu ndi ine, adatero iye. +Matenda atakula, gogoyu akuti adakomoka ndiye patsikuli adatengedwa ndi ena oyandikana nyumba kuti agone mnyumba mwawo. +Chisakasa cha Jemusi ndipo kumbuyoko ndi nyumba ya siwa28 Apa ndi pamene mudziwo udagwirizana kuti umumangire nyumba gogoyu koma malinga ndi nyakwawa Howa, izi sizidatheke. +Timafuna tipeze kaye udzu koma mpaka amwalira anthu tisadakumanebe kuti timumangire nyumba gogoyu. Mbale wawo mmodzi wotchedwa Mkwaso ndiye adadzazika timitengoti, idatero mfumuyo. +Pa 13 February akuti kudayamba mvula yosalekeza mpaka pa 15 ndipo mvulayinso akuti idamuthera pathupi gogoyu. +Gogoyo akuti adazizidwa kwambiri ndipo mmawa wa pa 15 adapeza kuti wamwalira. Koma abale adasonkhana ndi kuyamba mwambo wa maliro. +Koma chodabwitsa, thupilo akuti adalirowetsa mnyumba ya Felesita kuti anthu ayambe bwino kukhuza. Nsima yomwe wakhala akuisowa akuti idaphikidwa ndipo achibale adalira mosaleka. +Gulupu Mpochela idati anthu ena adakwiya kuona kuti banjali lidaganiza zolemekeza maliro kusiyana ndi munthu wamoyo. +Gogogyu wakhala akuvutika kwa nthawi yaitali. Adabwera kuno mu October mpaka wamwalira akugona panja opanda chakudya. Lero wamwalira ndiye amulowetsa mnyumba ya malata komanso paphikidwa chakudya, adatero iye. +Mpochela wati izi zakumukhumudwitsa ndipo aitanitsa banjali likamalira kulira malirowo. Uku ndi kulakwa, kuzuza munthu wamoyo choncho komanso wokalamba ngati uyo sibwino. Ndawaitanitsa ku bwalo langa, adatsimikiza Mpochela. +Gogoyu ali moyo adauza Msangulutso kuti ali ndi ana ku Lirangwe, koma pazolengeza za pamalirowo, abanja adati malemuwo sadasiye mwana ndipo mkazi wawo adamwalira. +Malinga ndi wachibale wina amene adakana kumutchula ndipo akukhala mumzinda wa Blantyre, malemuwa sadabereke mwana ndipo ana awiri amene amakhala nawo adali owapeza ndipo sadziwanso komwe anawo ali. +Nkhani zozuza anthu okalamba si zachilendo mdziko muno. Posakhalitsapa, anthu ena ku Neno adapha anthu anayi okalamba powaganizira ufiti. +Phwitiko: Kutambasula za maphunziro Unduna wa zamaphunziro udalonjeza zotukula maphunziro mdziko muno. Poyesetsa kukwaniritsa izi, undunawu uli ndi mapologalamu osiyanasiyana. Mmiyezi yapitayi undunawu udakonza zokweza fizi kuti uzitolera ndalama zokwanira zotukulira maphunziro. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi mneneri wa undunawu Rebecca Phwitiko: Phwitiko: Ndimalumikiza unduna ndi atolankhani Tafotokoza mbiri yako. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndine Rebecca Phwitiko, ndidabadwira ndi kukulira mumzinda wa Blantyre koma ndimachokera mmudzi mwa Danda, T/A Kalumbu mboma la Lilongwe. +Nanga mbiri ya maphunziro ako ndiyotani? Ndidaphunzira kusekondale ya Our Lady of Wisdom ku Blantyre mzaka za 1999 mpaka 2002 kenako nkukapanga maphunziro a ukachenjede ku Chancellor College. Panopa ndikuonjezera maphunzirowa kuti ndikhale ndi Masters Degree. +Udindo wako weniweni ku Unduna wa zamaphunziro ndi wotani? Kwenikweni ntchito yanga ndi yokhudzana ndi zofalitsa nkhani za undunawu. Ntchito yokonza zokhudza uthenga wopita kwa anthu, kulumikiza unduna ndi nyumba zofalitsa ndi kusindikiza nkhani, kukonza zochitika za unduna ndi kusanthula zomwe olemba ndi kufalitsa nkhani alemba ndi kulandira madandaulo ochokera kunthambi zosiyanasiyana ndi zina mwa ntchito zanga. +Usadalandire udindo umenewu unkagwira ntchito yanji? Ndinkagwira ntchito kuwayilesi ya boma ya Malawi Broadcasting Corporation (MBC) ngati mkonzi wa mapologalamu, muulutsi ndi mtolankhani. +Umagwiritsa bwanji ntchito nthawi yako yapadera? Ndikakhala ndi mpata ndimakonda kuwerenga mabuku okamba za Africa. Ndimakondanso kumvera nyimbo ndi kuyenda kuona malo osiyanasiyana. +Unduna wa zamaphunziro umanena kuti cholinga chake choyamba nkutukula maphunziro. Kodi mukuchitaponji pofuna kukwaniritsa zimenezi? Choyamba unduna wa zamaphunziro uli ndi udindo waukulu kuphunzitsa mtundu wa Amalawi. Udindo umenewu timagwirira ophunzira, aphunzitsi, makolo ndi ofalitsa komanso kusindikiza nkhani. Pofuna kukwaniritsa izi, tili ndi mapologalamu ambiri koma kuti onsewa atheke, mpofunika mgwirizano waukulu pakati pa ife ndi magulu onse omwe ndatchulawa ndipo mzati wake nkulumikizana pafupipafupi komanso moyenerera. +Okwiya aimitsa kumanga njanje Madzi achita katondo ku Nkaya mboma la Balaka komwe anthu okwiya aletsa kampani ya Mota Engil yomwe ikumanga njanje kumeneko kuti isiye kuthira dothi mminda mwawo komanso galimoto zawo zisadutsenso mmindamo. +Anthuwa ati sasintha ganizo lawo pokhapokha akuluakulu a kampani ya sitima zapamtunda mdziko muno omwe akumangitsa njanjeyi ya Central East African Railways (Cear) awapepese. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kuyambira Lolemba mpaka Lachitatu msabatayi, ogwira ntchito pakampu ya Nkaya adangogwira mchiuno kudikira kuti akuluakulu awo akambirane ndi kugwirizana ndi anthuwo asanayambe kupitiriza kugwira ntchitoyo. +Gulupu Nkaya adatsimikizira Tamvani Lachiwiri kuti anthu ake akwiya ndi zomwe anjanje akuchita pomatayira dothi mminda yawo popanda kukambirana kulikonse. +Panopa anthuwo akufuna amvetsetse kuchokera kwa omanga njanjewa pazomwe zikuchitikazo, adabwera kunyumba kwanga kudzandifotokozera koma nanenso ndalephera kumvana nawo ndipo ndawauza anjanjewo kuti aime kaye ntchito yawo mpaka titakambirana, adatero Nkaya. +Lachiwiri masana akuluakulu a Cear adakhamukira kumaloko kuti akakambirane ndi mfumuyo koma ngakhale Nkaya adatsimikizira anthuwo kuti ntchito iyambiranso, izi sizidachitike. +Malinga ndi mneneri wa Cear, Chisomo Mwamadi, mgwirizanowo udali woti pofika 2 koloko masana a Lachiwiri ntchitoyo ikhala itayambiranso. +Koma polowa kwa dzuwa Lachiwiri, ntchitoyo nkuti isadayambe, malinga ndi Nkaya. +Ndayesera kukamba ndi anthu anga onse amidzi ya Nsoma, Mbiya ndi Nkaya kuti awalole anthu agwire ntchito yawo, koma ndalephera. +Anthu akukana ndipo akuti pokhapokha a Cear awapepese [ndi kena kake osati pakamwa pokha] mpamene awalole kuti apitirize kugwira ntchito. Poyamba tidakambirana ndi akuluakulu a Cear ndipo tidagwirizana kuti tiwalole apitirize kugwira ntchito titagwirizana kuti tsiku lina abwera anthu ena kuchokera ku Cear kuti adzakambirane ndi anthuwo. +Mpaka lero palibe chogwirika tachiona nchifukwa chake anthuwa akukana kuti ntchito isagwiridwenso pokhapokha anthu amene adawatchulawo atabwera, idatero mfumuyi. +Koma mkulu wa Cear, Hendry Chimwaza, adati nayenso ndi wodabwa kuti mfumuyi ikulephera kulamula anthu ake kuti amvere zomwe adagwirizanazo. +Njanje si yathu, njanje ndi ya anthu ndipo mfumuyi ndi mboni kuti kubwera kwa chitukuko cha njanje kwabweretsa ntchito zambiri zotukula anthu ake monga kulembedwa ntchito ndi malonda kungotchulapo zochepa. Za malo otaya dothi komanso modutsa makina athu tidakambirana koma tikudabwa lero kumva nkhaniyi. +Mfumu kulephera kukambirana ndi anthu ake? Komabe tisathe mawu, tikambirana nawo ndipo ntchito ipitirira. Tikulankhula pano nkhaniyi taikamba kale ndipo kwatsala nkuona ntchitoyi ikugwiridwa, adatero Chimwaza Lachitatu. +Atafunsidwa ngati nkhaniyi akuidziwa akuluakulu a boma, Chimwaza adati idakali kaye mmanja mwawo ndipo ngati pena patavuta adziwitsa akuluakuluwa. +Kupatula kuthira dothi mminda, china chomwe anthuwa akudandaula ndi galimoto zikuluzikulu ndi makina awo zomwe zimadutsa mmindamo. +Mmodzi mwa anthuwo, amene adakana kutchulidwa dzina, adati mgwirizano wawo ndi anjanje udali woti alandira ndalama kuti galimotozo zizidutsa mminda mwawo komanso kuti azitayira dothi mdera lawo. +Poyamba amati angothira dothi mmalo amene minda yakokoloka ndipo dothilo athira ndipo akupitirizabe kuthira moti sitingalimenso nchifukwa chake tawaletsa, adatero. +Ntchito yomanga Nkaya siteshoni idayamba chaka chatha mu November ndipo gawo loyamba latha June chaka chino. +Chimwaza adati gawo loyamba lidali kumanga njanje zina ziwiri kuphatikizapo yakale yomwe idalipoyo, kukwanitsa zitatu. +Kumanga kwa njanjezi kuthandiza kuti sitima zitatu zizitha kupatukirana pa Nkaya popanda vuto lililonse komanso azitha kuchulutsa ndi kuchepetsa mabogi, zomwe sizimachitika poyamba. +Kusowa kwa madzi kusokoneza zambiri ku Lilongwe Chidziwitso cha Lilongwe Water Board (LWB), bungwe lopopa ndi kugawa madzi mumzinda wa Lilongwe, choti madzi akhala akuvuta kufikira dzinja chatsimikiza kuti ntchito zambiri, makamaka za umoyo, zisokonekera mumzindawu, womwe ndi likulu la dziko la Malawi. +LWB idalengeza sabata ziwiri zapitazo kuti iyamba kugawa madzi mosinira potengera mlingo wa madzi womwe kampaniyi ili nawo mmadamu ake awiri a Kamuzu 1 ndi 2. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Bungweli lidati pomwe madera ena azilandira madzi mumzindawu, kwina kuzikhala kopanda madzi ndipo izi zipitirira mpakana mvula ya chaka chamawa idzabwere. +Kuvuta kwa mvula kwachititsa kuti madzi achepe modetsa nkhawa mmadamu awiri a Kamuzu 1 ndi 2 omwe timasungiramo madzi. Madzi omwe alipo panopa sangapose theka la madzi omwe timafuna kuti tikwaniritse ntchito yathu, chidatero chikalata cha bungweli. +Madamuwa alibe madzi okwanira kaamba koti mvula sidagwe bwino komanso mitengo yomwe imathandiza kusunga madzi idatha mmphepete mwa mtsinje wa Lilongwe. +Timadalira madzi ochokera mumtsinje wa Lilongwe womwe umatsira mmadamu athu. Mtsinjewu umachokera mnkhalango ya Dzalanyama koma poti mitengo idatha mnkhalangomu, mtsinjewu uli pambalambanda ndiye madzi sachedwa kuuma, chidatero chikalatachi. +Mneneri wa chipatala chachikulu mumzindawu cha Kamuzu Central Hospital (KCH), Mable Chinkhata adati ngakhale kuti madziwo sadayambe kuvuta pachipatalachi, ali ndi nkhawa kuti zidzatha bwanji madzi akadzayamba kuvuta chifukwa ntchito zambiri pachipatalachi zidzasokonekera Ntchito zaumoyo, makamaka pachipatala, zimafuna madzi kwambiri. Mwachitsanzo, makina omwe timachapira zipangizo zochitira opaleshoni ngakhaleso zochapira zogonera ndi zofunda kapena makatani zimasiya kugwira ntchito madzi akangosiya chifukwa zimayendera kompyuta, adatero Chinkhata. +Iye adati makinawa salola madzi ochita kuthiramo, koma opopa okha kudzera mmakina a kompyuta, ndiye madzi akangosiya makinawa nawo amasiya kugwira ntchito. +Chinkhata adati nkhani ina yomwe ingavute ndi yaukhondo potengera kuti pachipatalachi palibe zimbudzi zokwanira zokumba moti odwala ndi owadikirira omwe amadalira zimbudzi zamadzi. +Timasunga odwala pafupifupi 1 000 patsiku ndiye ena pomwepo amakhala ndi owadikirira awiri kapena atatu. Mukawerengera ndi anthu angati amenewo? Tsono onse azigwiritsa ntchito zimbudzi zamadzi, chonsecho madziwo palibe, sikubala mavuto ena kumeneku? adatero Chinkhata. +Vutoli ndi lomweso anthu okhala mumzindawu omwe amagwiritsa ntchito zimbudzi za madzi aona ndipo ali nalo mantha kuti likhoza kubutsa matenda osiyanasiyana nkusokoneza ntchito zambiri. +Tangoganizani pamalo poti pali zimbudzi zamadzi zokhazokha popanda chokumba anthu akamva mmimba azipita kuti madzi atasowa kwa masiku awiri? Mapeto ake anthu akhoza kumapita mtchire kapena kungodzithandiza mtoileti nkusiyamo choncho. Poterepa munthu mmodzi kungodwala matenda ammimba ndiye kuti komboni yonse, adatero Innocent Mzungu, wa ku Falls mumzindawu. +Derali ndi limodzi mwa madera omwe nyumba zambiri zili ndi zimbudzi zamadzi ndipo zidamangidwa moyandikana. +Nkhani ina yomwe vutoli likhudze ndi la ulimi poti bungwe la BWB laletsa anthu okhala kumtunda kwa mtsinje wa Lilongwe omwe umatsira madzi mmadamu awo kuchita ulimi wamthirira. +Apa zikukolana ndi ganizo la boma loti anthu achilimike paulimi wamthirira polingalira kuti kakololedwe ka chaka chino sikadayende bwino, koma mlembi wamkulu muunduna wa zamalimidwe, Erica Maganga, adati ayambe wakambirana ndi kampaniyi kaye. +Choyamba sitikudziwa kuti ndi anthu angati amagwiritsa ntchito madamuwa kapena mtsinje wa Lilongwe paulimi wamthirira. Ndikuyenera kuti ndikambirane ndi akuluakulu a kampaniyi kuti tione pomwe pali vuto ndi momwe tingapangire, adatero Maganga. +Phungu wa kunyumba ya malamulo yemwe nkhalango ya Dzalanyama ili mdera lake, Peter Dimba, adati vutoli ndilochita kuweta chifukwa mzaka 10 mpaka 15 zapitazo atsogoleri adalibe chidwi choteteza nkhalangoyi. +Iye adati mzakazi, mitengo yambiri idadulidwa makamaka ndi anthu owotcha makala ndi ogulitsa nkhuni ndipo pomwe akuluakulu amadzidzimuka, madzi adali atafika kale mkhosi. +Mpanopotu pomwe zikukhala ngati akuluakulu akukhuzumuka. Muone chitumizireni asirikali ankhondo mnkhalangoyi zinthu zikusintha. Tsono ankalekeranji kuganiza zimenezi kalelo? adatero Dimba. +Iye adati ali ndi chikhulupiriro kuti ndi chitetezo chomwe chilipochi, chiyembekezo chili pa mphukira za mitengo kuwonjezera pa mitengo yomwe ikubzalidwa chaka ndi chaka. +Izi zili chonchi mumzindawu, makampani opopa ndi kugawa madzi mmizinda ya Blantyre ndi Mzuzu ati iwo alibe nkhawa ina iliyonse chifukwa mitsinje ndi madamu omwe amapopamo muli madzi okwanira. +Pakalipano, mkulu wa bungwe la anthu ogula ndi kugwiritsa ntchito malonda la Consumers Association of Malawi (CAMA) John Kapito adati ichi chikhale chitsegula mmaso kwa aliyense. +Iye adati mnyengo ino yakusintha kwa nyengo chilichonse chikhoza kuchitika ndiye mpofunika kuti mabungwe opopa ndi kugawa madzi akhale ndi malo ambiri komanso odalirika osungirako madzi kupewa mavuto ngati omwe agwa mumzinda wa Lilongwe. +Tizidziwa kuti madzi ndi moyo. Chilichonse chomwe munthu amapanga pamoyo wake chimalira madzi ndiye mpofunika kusamala kwambiri pankhani yokhudza madzi, osamachita zinthu modzidzimukira, adatero Kapito. +Ndinkacheza ndi mchimwene wake Akuti amapitapita kunyumba kwa namwali potengera chinzake chomwe chidalipo pakati pa iye ndi mchimwene wa namwaliyo. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Adagwiriziza kale unkhoswe: Emmanuel ndi Hawa Emmanuel Katiko akuti nthawi zonse amasowa tulo kulingalira za Hawa Mulele koma amalephera kumasuka powopa kuononga chinzake. +Tinkakhala limodzi ku Chiwembe mumzinda wa Blantyre ndipo mchimwene wake adali mnzanga koma ine maso adali pa mchemwali wakeyo adatero Emmanuel. +Iye adati mchaka cha 2009 ndipo adalimba mtima nkufunsira msungwanayo ndipo zidatheka mpaka madongosolo kuyambika. +Pa 7 November 2011 chinkhoswe chidachitika ku Chiwembe komweko ndipo akuti akuyembekezera ukwati woyera. +Iye adati adasangalatsidwa ndi Hawa chifukwa cha khalidwe lake lofatsa ndi lodzichepetsa komanso kudzilemekeza. +Hawa adati kwa iye kukwatiwa ndi Emmanuel ndi chinthu chapamwamba chomwe amalakalaka chitamuchitikira. +Zidayenda momwe ndinkafunira. Timakondana ndiposo ndi mwamuna wabwino woopa mulungu ndi wachikondi, adatero Hawa. +Awiriwa akuti akufuna Mulungu awatsogolere muulendo wawo wa banja kuti adzakhale limodzi mpaka kale popanda chosokoneza. +kwa Ngombe zamkaka zimalira chisamaliro chokwanira Lasford Mbwana ndi mmodzi mwa alimi a ngombe zamkaka omwe akuchita bwino kwambiri kwa Bvumbwe mboma la Thyolo. Moti mlimiyu akuyenda chokhala kaamba koti adagula galimoto kuchokera mu ulimiwu. BRIGHT KUMWENDA adacheza naye motere: Tafotokozani, kodi ulimi wa ngombe zamkaka mudayamba liti? Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ulimi wa ngombe zamkaka ndidayamba 2006 nditaona momwe anzanga amapindulira. Moti ngombe yanga yoyamba ndidagula K130 000 ndipo ndakhala ndikuonjezera mpaka zidafika 8. +Kodi mwapindula motani ndi ulimiwu? Mbwana kudyetsa ngombe zake zizipereka nkaka wochuluka Phindu ndi losachita kunena. Ndikadakhala kuti sindikupindula sindikadaonjezera chiwerengero cha ngombe zanga. Ngombe za mkaka zimandipatsa ndowe zothira kumunda, ndalama zogulira chakudya, zovala ndi zinthu zina zosoweka pabanja panga. Panopa banja langa likuyenda chokhala chifukwa choti tidagula galimoto kuchokera mu ulimi womwewu. +Nanga mungamulangize zotani munthu amene akufuna kuyamba ulimi wa ngombe zamkaka? Choyamba akhale ndi ndi chidwi ndi ziweto, malo wobzala nsenjere, amange khola labwino, akhale pafupi ndi madzi, komanso msika wa mkaka. +Kodi mukati khola labwino mukufuna kunena chiyani? Khola labwino limakhala ndi malo wodyera, wokamira mkaka, womwetsera mankhwala, wosewerera, wokhalira mwana akabadwa, woti ngombe izikhala panthunzi ikafuna kupuma kapena kugona. +Kodi patsiku mumakama mkaka wochuluka motani? Ngakhale ndili ndi ngombe 8 ndikukama zinayi zokha chifukwa choti zina ndi zazingono. Udzu, deya ndi masese zikamapezeka mosavuta ndimakama malita osachepera 100 patsiku omwe amandipatsa ndalama zokwana pafupifupi K500 000 pamwezi. +Chinsinsi choti ngombe izitulutsa mkaka wambiri nchiyani? Kudyetsa mokwanira, komanso mtundu wa ngombezo. Ngombe sizisiyana ndi munthu. Kodi simukudziwa kuti mayi akamadya mokwanira mwana wake amasangalala chifukwa choti mkaka umatuluka wambiri? Ngombe zamakono zimatulutsa mkaka wambiri pofanizira ndi zachikaladi. +Mukati ngombe zachikaladi mukufuna kutanthauzanji? Ukapereka umuna wa ngombe za Chizungu kwa ngombe zachikuda za Malawi Zebu, ana obadwa amakhala makaladisakhala azungu kapena achikuda. Amakhala a pakatikati. Moti mkaka omwe amatulutsa sukhala wambiri ngati wa ngombe ya Chizungu, komanso sukhala wochepa kwambiri ngati wa yachikuda. +Kodi ngombe zanu ndi za mtundu wanji? Ngombe zanga ndi za mtundu wa Holstein. Alimi ambiri a ngombe za mkaka mdziko muno akuweta ma Holstein, Jersey kapena ma Friesian. +Tafotokozani, kodi mumagula kuti ngombe zamkaka? Timagula kwa alimi anzathu. Ena amagula mmafamu a boma monga ku Mikolongwe ku Chiradzulu, Likasi ku Mchinji, Diamphwi ndi Dzalanyama ku Lilongwe ndi Dwambadzi ku Mzimba. Mabungwe a alimi a ngombe zamkaka a Shire Highlands Milk Producers Association (Shmpa), Central Region Milk Producers Association (Crempa) ndi Mpoto Dairy Farmers Association (MDFA) amathandizanso alimi kupeza ngombe zamkaka. +Nanga munthu asungire zingati akafuna kugula ngombe zamkaka? Zimatengera ndi wogulitsa, komanso komwe ukukagula ngombezo. Alimi ambiri amagulitsa ngombe pamtengo wapakati pa K250 000 ndi K300 000. Ikakhala yabere imafika mpaka K400 000. +Ndi mavuto otani omwe alimi a ngombe zamkaka amakumana nawo? Kusowa kwa madzi ndi zakudya makamaka miyezi ya pakati pa October ndi April. Nthawi imeneyi deya amasowa, komanso udzu umavuta kuwupeza. Moti alimi amayenda mitunda italiitali kuti apeze udzu wodyetsa ngombe zawo. Chaka chathachi thumba la deya tim0agula K6 000. Ngakhale adali wokwera mtengo, amavuta kupeza. Kuthimathima kwa magetsi kumawononga mkaka. Alimi a ngombe zamkaka amapanga magulu osiyanasiyana (bulking groups) omwe amasunga mkaka wawo mmalo ozizira, kudikira makampani kuti adzagule mkakawo. Magetsi akathima, mkaka ndi kuwonongeka asadadzautenge ndiye kuti alimi ali mmadzi. Kuphatikizira apo, mitengo yomwe makampani amatigulira mkaka ndi yotsika kwambiri. Ulimi wa ngombe zamkaka susiyana ndi wa fodya chifukwa wogula ndi amene amayika mtengo. +Ndi matenda otani omwe amagwira ngombe? Chifuwa chachikulu, chigodola, zotupatupa ndi ena mwa matenda omwe amazunza ngombe. +Nanga mawu anu otsiriza ndi wotani? Potsiriza ndikufuna ndipemphe anzanga kuti akumbe zitsime ndi kubzala nsenjere kuti asamavutike kupeza madzi ndi chakudya mudzinja. +Uve wanyanya mmisika Akugwiritsa madzi a mzithamphwi Tituluka mumsika munomabutchala Kafukufuku yemwe Tamvani wachita sabata ino waonetsa kuti uve wanyanya mmisika yambiri mdziko muno, maka ya mmakhonsolo a mizinda ya Blantyre ndi Lilongwe kaamba koti mulibe madzi a mmipope. +Masamba ngati awa amafunika kutsukaasanagulitsidwe Chifukwa cha kusowa ukhondo mumsika waukulu mumzinda wa Blantyre, mabutchala aopseza kuti ngati khonsolo sichitapo kanthu atuluka mumsikawu chifukwa akhala zaka ziwiri tsopano popanda madzi aukhondo. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Iwo akuti pakalipano akugwiritsa ntchito madzi amzithaphwi potsukira nyama ndi zipangizo zomwe amagwiritsa ntchito, pomwe ena akuti amachita kukagula madziwo kutali ndi malo a bizinesi yawo. +Izi zikhoza kuika miyoyo ya ogula ndi ogulitsa nyama pachiopsezo chifukwa nyama yosasamalika bwino ikhoza kukhala gwero la majeremusi omwe athanso kuononga miyoyo ya anthu odya nyamayo. +Koma mneneri wa khonsoloyi Anthony Kasunda wati khonsolo ya Blantyre sikudziwa kuti kumsikawu kudadulidwa madzi. +Kasunda: Tsatirani malamulo Timakhala ndi anthu oyanganira misika ndipo amenewo amalumikizana ndi khonsolo pa nkhani za mabilu a madzi ndi magetsi ndi zina zonse. Nkhani mukunenayi ndi yachilendo kwa ife, adatero Kasunda. +Loweruka sabata yatha, mabutchalawa adauza Tamvani kuti akhala akudandaulira khonsoloyi nthawi yaitali kuti ikonze zinthu koma palibe chomwe chikuchitika kupatula kulonjeza. +Iwo adati mu 2014, khonsoloyi idakazula mamita a madzi ponena kuti mabilu akukwera kwambiri, koma akuti adasiya lonjezo loti nkhani yokhudza madzi aikonza. +Butchala aliyense ali ndi chipinda chake chomwe amagulitsiramo nyama. Pomanga msikawu, chipinda chilichonse chidali ndi mpope wamadzi, koma mu 2014 khonsoloyi idadzazula mamita. Kuchokera apo mpaka lero tilibe madzi, adatero butchala wina. +Panopa tikugwiritsa ntchito madzi amene amangodzitulukira pansi pafupi ndi msikawu, pena timakagula mzigubu. +Iye adati poyamba akamalipira ndalama za lendi amaphatikizaponso za madzi malinga ndi bilu yomwe yatuluka ndipo khonsoloyi ndiyo inkakalipira ku Blantyre Water Board. +Sitimvetsabe chifukwa chomwe adachotsera madziwa, chifukwa timalipira, koma tidadabwa akudzachotsa mamita Achikhala amadzachotsa ndi a Water Board bwezi mwina titadziwa chifukwa chake, adatero. +Paganizo la mavendawa lotuluka kumsikawu, Kasunda adati malamulo oyendetsera mzinda wa Blantyre amaletsa kuchita malonda paliponse kotero ndi kuphwanya malamulo kutuluka mumsikawu. +Aliyense wochita malonda mumzinda wa Blantyre akuyenera kutsatira malamulo onse ndipo palibe chifukwa choti wina aphwanye malamulowo mwadala, adatero. +Kupatula nkhani ya madzi, mabutchala a mumsika wa Blantyre ati nkhani ina iwatulutse mumsikawu ndi anthu ena amene akugulitsa nyama mwachisawawa popanda zikalata. +Kukumabwera galimoto zitanyamula nyama ndi masikelo awo. Akumagulitsa nyama paliponse pamene ife amatikaniza kutero. Chifukwa cha izi, nyama yathu sikuyenda malonda. +Tadandaula koma sizikumveka. Anthuwa alibe zikalata zogulitsira nyama koma sakuletsedwa. Timadula chiphaso chophera nyama chomwe ndi K21 000, chipinda chogulitsira timalipira K17 000 pamwezi, koma ena akuwalola kumagulitsa nyama paliponse, adatero mmodzi wolankhulira mabutchalawo. +Pankhaniyi, Kasunda adati khonsolo sidapereke chiphanso cha bizinesi kwa ogulitsa nyama paliponse ndipo anthu amene amakhazikitsa bata mumzinda wathu [ma rangers] amalanda malonda alionse amene akuchitikira malo osayenera. +Nawo msika wa ku Limbe mumzindawu mavutowa aliponso chifukwa nakonso madzi adawadulira mu 2014. +Podula madziwo, khonsoloyi idatsegula malo amodzi amene anthu onse mumsika akutungapo. +Ku Lilongwe, misika ya Tsoka, Kawale, Biwi ndi Mchesi ukhondo ulipo kaamba koti madzi aukhondo aliko. +Koma mumsika wa Lilongwe Central womwe ndi waukulu, uve akuti wafikapo pamene mavenda akugwiritsa ntchito madzi amumtsinje wa Lilongwe. +Kondwani Juwawo, yemwe amagulitsa tomato mumsikawu, adati akafuna madzi abwino ndiye amakagula kwa munthu wina pafupi ndi msikawo. +Madziwa ndi odula chifukwa ndi a munthu osati a Water Board. Ngati tilibe ndalama timakatunga kumtsinjeko kudzatsukira tomato ndi kuwaza ndiwo zamasamba kuti zisanyale, adatero Juwawo. +Ku Mzuzu zinthu akuti zili bwinoko chifukwa misika ya Luwinga, Zigwagwa ndi msika waukulu wa Mzuzu mulibe mavuto a madzi. +Lachitatu Tamvani itazungulira misikayi, yomwe imakhala ndi anthu ambiri, zinthu zidaoneka zosinthirako pamene wamalonda aliyense adali ndi mwayi wa madzi aukhondo mmisikayo. +Mkulu woona za umoyo mumzinda wa Mzuzu, Felix Namakhuwa, adati misika yonse kumeneko ili ndi madzi monga njira imodzi yolimbikitsa nkhani za ukhondo. Timawalimbikitsa za kufunika kotsuka malonda awo komanso kusamba mmanja asadayambe kugulitsa malonda awo. Ichi nchifukwa chake venda aliyense ali ndi madzi mmisikayi, adatero Namakhuwa.Zowonjezera: Martha Chirambo ndi Steven Pembamoyo. +Anatchezera Sakuyankhanso foni Zikomo, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndine mtsikana wa zaka 19 ndipo ndidapeza bwenzi langa mu 2012. Poyamba ankalimbikira kuti andikwatire chaka chomwecho koma ndidakana. Kuyambira mu 2014 mpaka 2015 nkhani yake idali yomweyo kuti andikwatire koma ndidamuuza kuti andidikire ndingomaliza kaye sukulu. Koma kuchoka nthawi yomweyo adasiya kundiimbira foni ndipo ineyo ndikati ndimuimbire sayankhanso. Sindikudziwanso ngati ubwenzi wathu ukupitirirabe ndiye mundithandize pamenepa kuti nditani popeza ndinali naye yekhayo. +FR, Zomba. +FR, Zikomo, mwana wanga, pondilembere. Atsikana a maganizo ngako akowo okonda sukulu ndi ochepa masiku ano; ambiri akangofunsiridwa basi womwewo kukalowa mbanja. Iwe usadandaule kwambiri za chibwenzicho kuti kaya chatha kaya chilipo, koma ingolimbikira sukulu. Ndanena izi chifukwa ngati ukunena zoona kuti atangokufunsira mnyamatayo mu 2012 basi maganizo ake adali poti mukwatirane nthawi yomweyo, osaganizira za tsogolo lako pa nkhani ya maphunziro. Akadakhala mwamuna wachikondi chochokera pansi pa mtima akadamvetsa kuti maphunziro ndi ofunika kwambiri pamoyo wa munthu aliyense wofuna tsogolo lowala. Kuthamangira kukwatira kapena kukwatiwa si chanzeru; palibe phindu kukhala mbuli pamene uli ndi mwawi wa maphunziro. Ndiye ngati mnyamatayo wasiya kuyankha kapena kukuimbira foni, ndi mwayi wako umenewo kuti uike mtima wako wonse pamaphunziro mpaka umalize kenaka mpamene uziganiza za ntchito kapena banja poti maphunziro ndi zibwenzi nthawi zambiri siziyendera limodzichina chimasokonekera basi. Waonetsa kukhulupirika pokhala ndi bwenzi mmodzi yekhayo ndiye sindikukaika kuti udzatha kupeza mwamuna wokhulupirika womanga naye banja mtsogolomu ukapitiriza ndi mtima umenewo wopanda chimasomaso. +Umandiwaza Anatche, Gogo wanga ndiwe wanzeru ndipo umandizawaza. Ndidawerenga Msangulutso wa pa 7 February 2016 ndipo nkhani idandigwira mtima ndi yomalizayi yoti mwamuna anakaonekera kwawo kwa mkazi ndipo mkazi naye ati akufunanso kuti akaonekere kwawo kwa mwamuna. Nane mavuto amenewa ndili nawo ati mkazi akaonekere kaye kwathu kenaka ndipite kwawo ati kuti makolo anga akhale ndi chidwi choti adzamuone. Ndiye takhala tikulimbana ndiye pano ndinangozisiya chifukwa [zopanda pake] ndimadana nazo ngati kubanjako ndizikalandira salale PS, Blantyre. Hahahahaa! A PS ndinu woseketsa! Ayi, zikomo chifukwa cha maganizo anu, koma ndangoti tikumbutsane kuti nkhani za chikondi nzovuta ndipo zimafuna kufatsa nazo, kupirira ndi kumvetsetsana. Inu simunafumulire kungozisiya? Ndikhulupirira simunathetse chibwenzi ndi wokondeka wanu chifukwa cha nkhani yoti akufuna akaonekere kwanu kuti makolo anu akamuone komanso kuti akamudziwe. Kwa ena izi zilibe vuto malingana ndi kusiyana miyambo ndi zikhalidwe, koma kwa ena zoti mkazi naye akaonekere kwa makolo a mwamuna nzachilendo ndithu! Koma zonse zimatha nkukambirana basi. +Akuti tibwererane Gogo wanga, Ndidali paubwenzi ndi mnyamata wina kwa chaka chimodzi koma anathetsa chibwenzicho popanda chifukwa. Ine ndinapezana ndi wina amene timagwirizana kwambiri. Pano wakale uja akuti tibwererane. Kunena zoona wakale uja ndimamukondabe mpaka lero. Ndithandizeni, nditani pamenepa? Cyndie, Blantyre. +Zaka 14 kaamba kovulaza mkazi wake Juliyasi Dalasoni wa mmudzi mwa Zidana, T/A Phambala mboma la Ntcheu, amulamula kupita kundende kukagwira ukaidi kwa zaka 14 kaamba komenya ndi kuvulaza mkazi wake, Selina Juliyasi, modetsa nkhawa. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Malinga ndi umboni womwe udaperekedwa ndi apolisi mbwalo la milandu la majisitireti la Lilongwe, izi zidachitika pa 26 December 2015, kwa Biwi mumzinda wa Lilongwe. +Khoti lidamva kuti mnyamata wina adathamanga kukadziwitsa Christina Walasi kuti mngono wake, Selina, wavulazidwa koopsa ndi mwamuna wake. Ndipo Walasi mothandizana ndi anthu ena adamutengera kuchipatala cha Kamuzu Central komanso kudziwitsa apolisi. +Our cartoonists impression of GBV Lipoti la kuchipatala lidaonetsa kuti, Selina, yemwe akuti adamuwaza madzi otentha kunkhope komanso kumupondaponda pamimba mpaka kukomoka, adavulala kwambiri mmutu, kunkhope kudzanso kuthyoka nthiti. +Selina mpaka pano akulephera kukhala pansi, kuyankhula komanso kudya kaamba ka ululu. +Ndipo patsiku lozenga mlanduwu posachedwapa, bwalolo litamufunsa kuti ndi chifukwa chiyani iye adachita chiwembu choterechi kwa mkazi wake, Dalasoni, wa zaka 45, adayankha kuti mkazi wakeyo adamugwira akuchita chigololo ndi mwamuna wina, zomwe zidamuwawa kwambiri. +Podziteteza Dalasoni adafotokoza motere: Udali usiku wa pa 26 December 2015, pamene anthu adandiuza kuti akazi anga ali ndi mwamuna, choncho ine nditapita ndinakawapeza akupanga chigololo ndi mwamunayo. Atandiona mwamunayo adathawa, wamkazi adangophimba kumaso. +Nditawafunsa akazi anga kuti mukupanga chiyani, iwo anandigenda ndi njerwa ndi kundimenya, choncho inenso ndinawamenya ndipo adakomoka, ine ndinangochokapo zitatero. +Koma atamufunsanso kuti abweretse umboni ooneka ndi maso pazomwe akunenazo, iye adangoti kukamwa pululu kusowa choyankha. +Pachifukwachi, wapolisi Euginio Yotamu, adapempha bwalolo kuti Dalasoni ayenera kulandira chilango chokhwima zedi kaamba kakuti mlandu womwe adapalamulawo ndi waukulu malinga ndi gawo 235 la malamulo ozengera milandu mdziko muno. +Anatchezera Ndimamukonda Agogo, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndinali pachibwenzi ndi mkazi wina ndipo zaka ziwiri zatha pomwe tinasiyana. Pano ali ndi mwana yemwe wabereka mwezi watha ndiye akumabwera kwa ine nkumati tibwererane. Kodi pamenepa ndithani, agogo? Mkaziyo kunena zoona ndimamukonda, koma pano ndinalimba mtima. Nditani? Ine Amfumu, Zingwangwa Amfumu, Nkhani yanu ndi yovuta kuitsata bwinobwino chifukwa simukumasula kuti vuto lanu ndi chiyani kwenikweni. Poyamba mwanena kuti mkaziyo munasiyana naye zaka ziwiri zapitazo, munasiyana chifukwa chiyani? Mwati pano mkaziyo akuti mubwererane ndipo inu nomwe mukuti kunena zoona ndimamukonda. Komanso inu nomwenso mukuti pano munalimba mtima, mukutanthauzanji? Mwatinso mkaziyo ali ndi mwana wa mwezi umodzi, nchachidziwikire kuti mwanayo si wanu-poti mwanena nokha kuti chibwenzi chanu chidatha zaka ziwiri zapitazo. Apatu, kunena zoona, Amfumu, mayankho muli nawo ndinu. Ngati mkaziyo mukuti mumamukonda, chovuta nchiyani kuti mubwererane? Koma mukuti mwalimba mtima, kulimba mtima kotani? Nchifukwa chake ndikuti zonse zili ndi inu kuti mubwererane kapena ayi poti zifukwa zake zomwe mudalekanirana mukuzidziwa ndinu. Mwakula mwatha, Amfumu. +Akungosereulana nane? Anatchereza, Ndili pachibwenzi ndi mtsikana wina amene ndikufuna kukwatira koma zochitika zake zikundidabwitsa. Chaka chatha adandijejemetsa pamene adati ali ndi mimba ndipo amati akufuna achotse chifukwa akuopa makolo ake. Ndidamuuza kuti asayerekeze kuchotsa pathupipo chifukwa ine ndidali wokonzeka kumukwatira, zivute zitani. Kenaka, patapita kanthawi adati amangocheza, alibe mimba. Mwezi wathawu adandiza kuti adakayezetsa magazi ndipo amupeza ndi kachilombo ka HIV ndipo nkofunika kuti nane ndikayezetse. Kunena zoona, sindinapite kukayezetsa koma ndidangomunamiza kuti ndakayezetsa ndipo sanandipeze ndi kachilombo. Pano wandiuza kuti amangonama, sadakayezetse magazi. Kodi iyeyu ndi mtsikana wotani? Ndipitirize naye chibwenzi? YB, Lilongwe Zikomo YB, Pali zinthu ziwiri: Bwenzi lakolo mwina ndi wokonda kusereula komanso mwina ndi kamberembere. Koma zili ndi iwe kupeza choona chenicheni mwa iye. Koma tiyeni tione mbali zones ziwirizi. Poyamba, ngatidi amakonda kusereula, umuuze kuti pali zina zoti angathe kusereula nawe koma nkhani za mimba ndi HIV si nkhani zosereula nazo. Ngati akufuna aone ngati umamukondadi pali njira zina, osati kunamizira mimba kapena kuti amupeza ndi kachilombo. Kusereulana si kolakwika mukakhala pachibwenzi chifukwa ndi njira ina yokometsa chibwenzi chanucho, koma pali malire. Komanso mwina, monga ndanena, akhoza kukhalanso kamberembere ameneyo. Nkutheka mwina adachotsadi mimba ameneyo. Ngati adaterodi, cholinga chake chidali chotani? Wofuna banja amachotsanso pathupi mwadala? Ayi. Tsono pankhani yokayezetsa magazi, bwanji mutapita kuti mukayezetse limodzi kuti mudziwe momwe mulili nonse? Kwa anthu ofuna banja lansangala, losakaikirana, kuyezetsa magazi ndi njira imodzi yothandiza kuti mudziwe ngati muli ndi kachilombo pena ayi. Mukatere mumadziwa chochita pankhani ya kasamalidwe ka banja lanu. +Kutambasula nthenda ya kadzamkodzo Kunjaku kuli nthenda zosiyanasiyana koma nthenda zina ukamva, kudulitsa mutu wazizwa. Sabata yapitayi, nduna ya zaumoyo, Dr Peter Kumpalume, adatsogolera Amalawi kutsegulira nyengo yokumbukira matenda a kadzamkodzo (Fistula) mboma la Kasungu. STEVEN PEMBAMOYO adachita chidwi ndi nthendayi ndipo adacheza ndi ndunayi, yomweso idagwiraponso ntchito ya udokotala, kuti itambasule za nthendayi motere: Kumpalume kutsindika za vuto la kadzamkodzo Anduna, anthu akudziweni. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ndine Dr Peter Kumpalume, nduna ya zaumoyo, komanso phungu wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) kudera la kumadzulo kwa boma la Blantyre. Ndagwirapo ntchito zachipatala mmadipatimenti osiyabnasiyana mdziko muno ndi maiko akunja. +Kodi apa mukuti pakuchitika zokhudza kadzamkodzo, chimenechi nchiyani? Iyi ndi nthenda yoopsa kwambiri koma anthu ambiri sazindikira. Nthenda imeneyi imagwira amayi ndipo mzimayi akagwidwa ndi nthenda imeneyi, moyo wake umasinthiratu. Amadutsa mchipsinjo chachikulu, makamaka chifukwa chosalidwa ndi amayi anzake ngakhale abambo apakhomo, moti ena banja mpaka limatha. +Amasalidwa mnjira yanji, kapena matendawa ndi opatsirana? Ayi, matendawa si opatsirana koma amayamba malingana ndi zichitochito zina pamoyo wa munthu, makamaka pazokhudzana ndi uchembere. Mayi amagwidwa ndi matendawa malingana ndi momwe wayendetsera moyo wake wa uchembere, koma palibe mwayi woti wina akagwidwa akhoza kupatsira anzake, ayi. +Ndiye chomusalira nchiyani? Poyamba mukuyenera kumvetsetsa kuti nthendayi ndi nthenda yanji ndipo imachita zotani. Imeneyi ndi nthenda yokhudza njira ya amayi. Pazifukwa zina, njirayi imapezeka kuti yabooka ndiye mkodzo ukamabwera umangodutsa nkumachucha, mwinanso nkusakanikirana ndi chimbudzi. Pachifukwachi, mzimayi amamveka fungo kwambiri moti pagulu la anzake amasowa mtendere komanso anzake amamuthawa. Chomwechomwechonso, abambo a kunyumba amatha kupirira kwa kanthawi koma pena amatopa nkuchoka pakhomopo. Si nkhani yamasewera, ayi, makamaka kwa mayi yemwe wagwidwa ndi matendawo. +Mwangoti pazifukwa zina, kodi simungatambasuleko zina mwa zifukwazo? Ndikufotokozerani zifukwa zitatu zomwe ndi zikuluzikulu muno mMalawi. Pali uchembere olawirira. Munthu akatenga pakati ali wamngono, ziwalo zake zimakhala kuti sizidakhwime ndiye chifukwa chokakamiza pobereka, vuto lotere likhoza kubwera. Njira ina nkubereka pafupipafupi, ziwalo zimatopa mpaka nthawi imadzakwana yoti vuto laonekera komanso njira ina ndi kukonda kuchirira kwa azamba chifukwa pakabwera vuto panthawi yochira, azamba amalephera machitidwe ake. +Ndiye mwati vutoli ndi lalikulu mdziko muno, palibe njira yothandizira amayi oterewa? Njira ilipo yomwe nkuthamangira kuchipatala basi. Mdziko muno muli zipatala zingapo komwe kuli madipatimenti othandiza pavutoli koma anthu ambiri amatsogoza kuti matendawa amabwera kaamba kolodzana moti amataya nthawi nkumayendayenda mwa asinganga mmalo moti athamangire kuchipatala akalandire thandizo zinthu zisadafike poipitsitsa. +Nanga kungoti zipatala, osatiuzako kuti ndi kuti kuli zipatalazo? Zina mwa zipatala zomwe zikupereka nawo thandizo kwa amayi omwe ali ndi nthendayi ndi Queen Elizabeth Central Hospital (Quech) mumzinda wa Blantyre, Zomba Central Hospital ku Zomba, Bwaila ku Lilongwe, Mzuzu Central Hospital ndi Monkey Bay. +Zokhudza mikangano ya ufumu Nkhani za ufumu zakhala zikuvuta kwa nthawi yaitali. Zina mwa nkhani zomwe zakhala zikupanga mitu ndi mikangano ya ufumu komanso pakati apo kudabuka ganizo loti mmatauni musamakhale mafumu STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Gulupu Santhe imodzi mwa mafumu akale. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndikudziweni mfumu. +Santhe: Makhoti asamalowererepo Ndine Aclas Chisoni koma la ufumu ndine nyakwawa Santhe wa mdera la T/A Kalolo ku Lilongwe. +Tiziti a Santhe ake ndi a ku Kasunguwa? Chibale chilipo koma chakumizu. A ku Kasungu ndi a mbere la a Nkhoma pomwe ife a kuLilongwe ndife a mbere la a Mwale. +Ufumu mudaulowa liti? Ndidalowa ufumu mchaka cha 1985 achimwene anga a Wilson Pwela omwe adali afumu atamwalira mchaka cha 1983. Panopa ndikutha zaka 21 ndili mfumu ndipo chaka chino ndikuyembekeza kukwenzedwa kufika pa Senior Group Santhe. +Pa zaka zonsezi mwakhala mfumu, ndi mavuto anji omwe mungatiuze kuti amapezeka mu ufumu? Mavuto alipo ambiri osayiwala mikangano. Maufumu ambiri amatchuka ndi mikangano makamaka yemwe adali nfumu akamwalira ndiye kuti wina alowepo. Nthawi zina mpaka pamalowa za mankhwala kulimbirana ufumu. Vuto lina ndilakuti adani amachuluka chifukwa ukangoweruza mlandu, yemwe sizidamukomere basi chidani chimayamba pomwepo. +Ndiye pakatipo kudabuka zoti maufumu a mtauni athe, maganizo anu ngotani? Sizowona ayi mafumu ndiwofunikabe paliponse. Chitukuko kuti chiyende ndi mafumu, pakagwa zovuta mafumu ndiwo amaongolera zonse. Palibe kanthu kuti ndi mtauni kapena kumudzi koma pomwe pali anthu pamayenera utsogoleri. +Makhansala sangagwire ntchito ya mafumu? Inu tiyeni tiziganiza mozama. Mfumu amasankha munthu okhwima maganizo odziwa ndi kutsata mwambo ndi chikhalidwe tsono makhansala ambiri amasankhidwa kaamba ka maphunziro kapena kutha kulankhula basi. Utsogoleri wa ufumu sachita kampeni ayi anthu okha amaona kuti uyu atithandiza. +Nanga nkhani za ufumu kupititsa mukhoti? Ukunso nkusokoneza chifukwa nkhani ya ufumu imayenera kukambidwa kumudzi apo ayi kwa DC ndipo zikavutitsitsa ku unduna wa zamaboma angonoangono ngati kholo la maufumu. +Amukwenya ponena olumala kuti agalu Banja lina lapempha mkulu woyanganira za maphunziro mmaboma a Phalombe, Mulanje ndi Thyolo (Divisional Education ManagerDEM) kuti athane ndi mphunzitsi wina amene akumuganizira kuti adanena ana olumala pasukulu ya sekondale ya Phalombepo kuti ndi agalu. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kalata yomwe tapeza, yatumizidwanso kwa wachiwiri kwa mkulu woyendetsa maphunziro a ana olumala, mkulu wa sukulu ya Phalombe, mkulu wa bungwe la anthu amene ali ndi vuto la kumva la Malawi National Association for the Deaf (Manad), mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a anthu olumala la Federation of Disability Organisations in Malawi (Fedoma) ndi ena. +Malinga ndi kalatayi, mpunzitsiyo akuti adachita izi pa 2 February pamene banjalo lidapita kukaona mwana wawo. +Kalatayo, yomwe walemba ndi mmodzi mwa a pabanjapo, Bettie Chumbu, yati patsikulo iwo atafika pasukulupo adakumana ndi wophun-zirayo ndipo adali ndi ophunzira anzake a mavuto osiyanasiyana achibadwidwe. +Sukuluyi, malinga ndi mphunzitsi wamkulu, James Kamphonje, ili ndi ophunzira azilema zosiyanasiyana monga achialubino, osamva, osalankhula ndi ena. Onse pamodzi akuti alipo 15. +Chumbu adati akucheza ndi ophunzirawo mpamene mphunzitsiyo adatulukira, botolo la mowa lili mmanja nkunena mawu amene adawakwiyitsawo. +Adati, mukuchita chiyani ndi agaluwa?, adatero Chumbu. Akuti adamufunsa mphunzitsiyo zomwe ankatanthauza ponena mawu amenewo, koma iye akuti adabwereza mawuwo, amvekere: Yes these are dogs [Inde, awa ndi agalu]. +Gwen Mwamondwe, yemwe ankayendetsa galimoto yomwe adakwera Chumbu popita kusukuluko ndi Hussein Chindamba, yemwe adatsagana ndi nawo paulendowo, adatsimikiza za nkhaniyi ponena kuti adayesetsa kuuza mphunzitsiyo kuti zomwe wayankhula zidali zopanda mutu ndipo ayenera kupepesa, koma akuti zidakanika mpaka ana asukulu ena ndiwo adalowererapo nkumududa pamalopo. +Koma Lachiwiri Msangulutso utafuna kumva mbali ya mphunzitsiyo, adangoti: Tilankhulane cha mma 5 koloko kuti ndiyankhepo. Koma titamuimbira kangapo, iye sadayankhenso foni. +Kumbali yake, Kamphonje adati nkhaniyi ili pakati pa banja lodandaula ndi mphunzitsiyo ndipo mbali ziwirizi zikukambirana. +Chomwe ndikudziwa nchakuti banja lodandaulalo likukambirana ndi Malikebu, zomwe agwirizane timva kwa iwo, adatero mphunzitsi wamkuluyu amene adakana kulankhulapo zambiri. +Titamufunsa Chumbu ngati akukambirana ndi mphunzitsiyo, iye adati: Nkhani tidaisiya mmanja mwa akuluakulu ndiye palibe chifukwa choti tiyambe kukambirana ndi mphunzitsiyu. Koma wakhala akundiimbira foni kuti tikambirane. +Mafoni amene akuimba sindikuwayankha ndipo mmalo mwake adanditumizira uthenga wapafoni kuti ndikupepesa kuti mundikhululukire. Ndikukudikirirani kuti ndidzapepese pamaso. Chonde ndikhululukireni, sizidzachitikanso, Mulungu akudalitseni. +Mkulu woyanganira maphunziro mmaboma a Thyolo, Mulanje ndi Phalombe, Christopher Nauje, adati akudikira lipoti kuchokera kwa banja lolakwiridwa. Ndidalankhuladi palamya ndi abanja lodandaula pankhaniyi ndipo ndidawauza kuti atumize dandaulo lawo kuofesi yathu polemba kalata. Panopa ndikudikirabe kalatayo ndiye sindingayankhepo kanthu, adatero Nauje. +Mkulu woona za maphunziro a olumala muunduna wa zamaphunziro, David Njaidi, adatsimikiza kuti walandira dandaulo kuchokera kubanja lodandaula ndipo wati akhala pansi kuti aone chomwe angachite. +Apa chatsala nchakuti tikambirane ndipo tipereke zomwe tapeza komanso zomwe tingachite ndi mphunzitsiyo, adatero Njaidi. +Blantyre yawala, iwalirabe Kuyenda usiku tsopano sikukhalanso koopsa ganizo la khonsolo ya mzinda wa Blantyre lipherezeke. +Mneneri wa khonsoloyi, Anthony Kasunda, wati khonsolooyi ikuganiza zoika magetsi mmisewu kuti aziwala usiku wonse mumzindawu. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mmbuyomu ena adaba zitsulo za magetsi Kasunda wauza Tamvani kuti pasadathe miyezi 6 msewu wa Masauko Chipembere Highway ukhala ndi magetsiwa kuchoka ku Blantyre mpaka ku Limbe. +Anthu aona kuwala ndithu. Ife talowa mumgwirizano ndi bungwe la Roads Fund Administration kuti tigwire ntchito imeneyi, yomwe idye ndalama zokwana K400 miliyoni, adatero Kasunda. +Iye adati mmisewu ina ingapo ntchitoyi yagwirika kale. +Tapanga kale kuchoka pa Kandodo Corner Shop mpaka pa Kameza Roundabout; Kwacha Roundabout mpaka pa Kudya kudutsa MBC TV, CI mpaka Green Corner; ndinso Sunnyside mpaka ku Manyowe. +Ntchito imeneyi yatitengera ndalama pafupifupi K145 miliyoni, zomwe ndi gawo la K1.8 biliyoni zochokera kuboma za ntchito yachitukuko cha mumzinda wa Blantyre, adatero Kasunda. +Mneneriyu adatinso khonsolo ikamapeza ndalama, ionetsetsa kuti misewu yonse ya mumzinda wa Blantyre ikhale ndi magetsi. +Magetsi amathandiza kukhwimitsa chitetezo. Ndikhumbo la khonsolo ya Blantyre kuti mzinda ukhale wowala usiku. Tikumema anthu onse a mumzindawu kuti atithandize poteteza magetsi amenewa, makamaka potsina khutu apolisi kapena akulu a khonsoloyi akaona wina akuononga dala zipangizo zamagetsi monga mapolo ndi nthambo zamagetsi, adaonjezera Kasunda. +Kalindo walasa! Akulu akale adati kulasa mtengo nchamuna chomwe. Makono tikhoza kunena kuti kuyenda pamsewu utavala mwado nkuvula komwe! Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndawala ya bunobwamuswe yomwe idali mkamwamkamwa sabata zingapo zapitazo mdziko muno idalephera kuchitika monga momwe ambiri ankaganizira, koma oyendawo adayendabe atabisa kumaso atavala mosadzilemekeza kwenikweni, koma uthenga wawo udafikabe kwa omwe umayenera kupita. +Kuvulatu si chinthu chachilendo, koma kutero pagulu nkumayenda pamsewu thima lili zii ndiye kuti pena pake zaipa. +Pofuna kutsimikizira Amalawi ndi atsogoleri a dziko lino kuti mdziko muno mwaterera ndi mchitidwwe wachilendo malinga ndi kusowetsedwa ndi kuphwedwa kwa anthu achialubino kwawanda masiku powaganizira kuti ziwalo ndi mafupa awo ndi zizimba zokawira chuma, phungu wa kumwera kwa boma la Mulanje Bon Kalindo, adakonza ndawala yowe adamema anthu kuti ayende ali chinochino mumzinda wa Lilongwe Lachinayi lapitali. +Kalua (kumanzere) kulandira chikalata kwa Kalindo atafika ku Nyumba ya Malamulo Momwe nthawi imati 8 koloko mmawa, anthu adali atayamba kale kusonkhana pa Roundabout yaku Area 18A pomwe ndawalayo idayambira ulendo wa ku Nyumba ya Malamulo kukapereka chikalata cha kuonetsa kukhumudwa ndi mchitidwewu komanso pofuna kukakamiza boma kuti likhimitse chitetezo kwa maalubino ndi kupereka chilango cha diso-kwa-diso kwa omwe apezeke ndi mlandu wopha anthuwa. +Anthu oyenda pagalimoto zawo ndi mmaminibasi amangoti suzisuzi mmawindo kuti aone yemwe ayambitse kuvula zovala zake potsegulira ndawalayo koma amadziwiratu kuti sizitheka poona mtsogoleri wa ndawalayo, Kalindo, ali mkabudula wamkati ndi malaya odula manja, zonse zofiira. +Otsatira ambirinso adavala zofiira ndipo ambiri adali mmakabudula ndi zodula manja kapena kwakwalala kumtunda. +Ngati woyambitsa wavala choncho ndiye kuti palibepo zovula apa. Mwina agwirizana kuti kuvula kwake kukhale komweku osati mpakana maliseche enieni ngati mmene amanenera, adatero Innocent Mose, mmodzi mwa anthu omwe adacheza ndi Msangulutso. +Zopatsa chidwi zambiri zidaoneka ndawalayo itayambika pomwe anthu ambiri amakhamukira kumdipitiwo, zomwe anthu ena sadayembekezere polingalira kuti pomwaza uthenga wa ndawalayo amati obwera akuyenera kudzabwera ali psatapsata. +Nyimbo, kuvina ndi kuseka, uku ena atanyamula zikwangwani zolemba mawu osiyanasiyana otanthauza kusakondwa ndi kuphedwa komanso kusowetsedwa kwa maalubino ndizo zidakunga ndawalayo, yomwe idakathera pachipata chachikulu cha Nyumba ya Malamulo komwe oyendawo adapereka chikalata chawo kwa wachiwiri kwa wapampando wa komiti ya zamalamulo mNyumbayi, Kamlepo Kalua. +Asadapereke chikalatacho, Billy Mayaya, mmodzi mwa omenyera ufulu wa anthu yemwe adali nawo pandawalayo, adawerenga chikalatacho ndipo atangomaliza padali kuimba ndi kuvina. +Kumayambiriro a sabata yathayi, ndawalayi isadachitike, nduna ya zofalitsa nkhani Patricia Kaliati idanenetsa kuti boma lilibe maganizo obwezeretsa chilango cha kunyonga anthu opezeka ndi mlandu wakupha potengera pangano la maiko onse. +Dziko la Malawi lidasayina nawo mapangano ambirimbiri okhudza za ufulu wa anthu ndiye sitingabwerere mmbuyo nkuyamba kuphwanya pangano lomwe tidasayina tokha, adatero Kaliati polankhula ndi atolankhani ku Nyumba ya Malamulo. +Koma mu 2014, dziko la Malawi lidauza msonkhano wa nthambi ya United Nations yoyanganira za maufulu a anthu ku Geneva, Switzerland kuti boma lilibe maganizo ochotsa chilangochi mmalamulo ake. +Mwa mfundo zina, chikalatacho chidati mchaka cha 1994, Amalawi adasankha kuti chilango cha diso-kwa-diso chipitirire ngati njira yochepetsera zophana ndiye sangalole kuti aziyendera maganizo a maiko ena. +Chomwe tikufuna nchakuti Nyumba ya Malamulo ichotse chiletso choperekera chilangochi kuti anthu onse opezeka ndi ziwalo kapena kupha maalubino komanso milandu ya nkhanza zofanana ndi zimenezi azilangidwa mokwanira, chidatero chikalatacho. +Zina zomwe amafuna anthuwa nzakuti apolisi apatsidwe mphamvu ndi zipangizo zokwanira zogwirira ntchito; pazikhala chilungamo pofufuza ndi pogamula nkhani zokhudza maalubino; komanso kuti nkhanizi zizikagamulidwa kubwalo loyenera. +Ndipo ngati kuti adachita kupangana, aphungu a Nyumba ya Malamulo masana a tsikulo (Lachinayi) adadutsitsa Bilu yoti pazikhala chilango chokhwimitsita kwa onse opezeka ndi milandu yopha maalubino komanso kuchotsa chindapusa kwa onse opezeka ndi mafupa kapena ziwalo za anthu. +Woganiziridwa kutsatsa mafupa a munthu agwidwa Bambo wa zaka 25, James Kanjira, ali mchitolokosi pomuganizira kuti amachita bizinesi yogulitsa mafupa a munthu mboma la Nkhotakota. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mkuluyu akuti adamugwira akutsatsa mafupa omwe akuganiziridwa kuti ndi a alubino. +Apolisi mboma la Nkhotakota atsimikiza kuti adamanga Kanjira Lachitatu pa 27 April, 2016 pomuganizira mlanduwo pamene akuti amayembekezera kulandira ndalama za malondawo kuchokera kwa kasitomala wake, Stanley Kambewa, yemwe adali atawatsina khutu. +Tamangadi James Kanjira yemwe amatsatsa mafupa a munthu. Iye adati mafupawo adali ku Kasungu. Polingalira zomwe zidachitika mbomali sabata yatha kuti alubino adaphedwa, woganiziridwayu tamutumiza ku Kasungu kuti akamufufuze bwinobwino, adatero mneneri wa polisi mboma la Nkhotakota, Williams Kaponda. +Woganiziridwayo: Kanjira Apolisi mboma la Kasungu atsimikiza za kumangidwa kwa Kanjira ndipo ati mkuluyu adali mmodzi mwa anthu omwe amafunidwa ndi apolisi poganiziridwa kuti akukhudzidwa ndi kusowa komanso kuphedwa kwa alubino wa zaka ziwiri mbomali. +Tidatumiza uthenga mmaofesi onse a polisi a maina a anthu omwe tikufuna ndipo atabwera naye Lachitatu, lapitali tidamupana mpaka adaulula komwe kudali anzake ndipo tidawagwiranso komanso adalondola komwe adakwirira mafupawo, adatero wachiwiri kwa mneneri wa polisi ku Kasungu Harry Namwaza. +Kanjira, yemwe amachokera ku Kasungu, akuti adapita ku Nkhotakota komwe adakumana ndi Kambewa nkumutsatsa malonda a mafupa a munthu ndipo atagwirizana, wotsatsidwayo adakauza apolisi za nkhaniyo. +Kaponda adati Kanjira ataona kuti malonda atheka, adamasuka nkuulula kuti mafupawo adali a alubino ndipo adali ndi mnzake yemwe panthawiyo adali ku Kasungu. +Iye adati wotsatsidwayo atamva zimenezo nthumanzi idamugwira polingalira kuti sabata yatha nkhani ya alubino wophedwa mboma la Kasungu idatchuka ndipo apolisi ali kalikiriki kusakasaka omwe adachita chiwembucho. +Munthu ameneyu adachita bwino kwambiri chifukwa popanda anthu ngati iyeyo, ife sitingadziwe kalikonse ndipo tikufuna anthu ambiri ngati awa atamatithandiza choncho, adatero Kaponda. +Iye adati mlanduwu padakalipano ndi wa mchitidwe omwe ukhoza kuyambitsa chisokonezo, womwe chilango chake chachikulu ndi miyezi itatu mndende potengera malamulo a dziko lino. +Koma Kaponda adati mlanduwu ukhoza kusintha chifukwa akumuganizira kuti adachita kufukula munthu wakufa, womwenso ndi mlandu paokha, koma zikadzapezeka kuti adachita kupha munthuyo, mlandu udzakhala wakupha, womwe atapezeka wolakwa akhoza kukaseweza kundende moyo wake wonse. +Nkhaniyo ili mkamwamkamwa, bungwe la Amnesty Internationa ladzudzula dziko la Malawi chifukwa cholephera kupereka chitetezo chokwanira kwa maalubino. +Mwachitsanzo, mwana angabedwe bwanji mnyumba usiku apolisi nkulephera kufufuza mpaka mwana kuphedwa? Ndi moyo wa munthu tikukamba apawu, osati chomera ayi, ndiye pamayenera kuchitika zakupsa, chatero chikalata cha chidzudzulo chomwe bungweli latulutsa. +Mchikalatacho, zadziwika kuti kuyambira mu 2014, anthu 12 achialubino aphedwa ndipo anthu asanu ndiwo akusowabe mpaka pano. Anthu 45 ndiwo adamangidwa pamilandu yokhudzana ndi kuphedwa kapena kusowa kwa anthuwa. +Koma nduna ya zachitetezo, Jappie Mhango, wati dziko la Malawi likuyesetsa kuchita zoti anthu amtunduwu komanso anthu omwe amaoneka ngati alibe mawu azitetezedwa mokwanira. +Mowe Pati: Amuna ndi dothi Tsikulo, mkulu wina adati tipite mtauni tikaone umo zikukhalira chifukwa mikangano ya oitanira basi komanso oyanganira mzinda ikukhala bwanji. Tidafika kumasitandi kumenetu kudali nkhondo yaikulu ati kulimbirana kuti amaminibasi ziwathera bwanji. Kodi azilipira kuti? Vuto lidalipo ndi lakuti kodi oyendetsa minibasi ndi mabwana awo, angakhale ndi zikwanje zakuthwa ndani? Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Zitayeni. +Lidali tsiku la amayi padziko lonse ndipo tidakhala malo aja timakonda pa Wenela. Adatulukira Mowe Pati kuchoka kwawo kwa Mkando, apooo! Kweeni, munasowatu zedi. Zikuyenda bwanji? adafunsa Gervazzio, wapamalopo. +Ndilipo. Kodi mwakumbuka zija ndinkanena za agalu athu ndi zothamangitsa anthu a ku China? Zija ndinkanena kuti atibwezere agalu athu. Ndidali mwana masiku amenewo, adatero Mowe Pati. +Koma mwati amuna ndi chiyani? adafunsa Abiti Patuma, uku akumvera nyimbo ya Nilibe Pulobulemu. +Abale, amuna ndithu ndi dothi. Ndipo musamawatchule kuti amuna ndi ana monga mwakhala mukunenera. Zitheretu, adatero Mowe Pati. +Inu, ndithu kumanja kudali Coca-Cola, koma ankamwa Fanta munthu wa mayi. +Aaaaargh! Mowe, mukunena zoona? Munganene kuti amuna ndi dothi? Chifukwa chiyani? adafunsa Abiti Patuma. +Eya, amuna ndi dothi, nanga si Mulungu adawalenga kuchoka kudothi! adayankha. +Koma kuganiza kwinaku ungamangoti munthu uyu amasuta wamkulu fodya. +Tsono mukatero, ndiye kuti bambo a kunyumba aja nawonso ndi dothi? Nanga ana anu aamuna aja nawonso ndi dothi? ndidafunsa. +Mwati bwanji? adafunsa Mowe Pati. +Ndikuti, mukamati amuna ndi dothi mukutanthauza kuti uja adaimba nyimbo ya Nilibe Pulobulemu mokopera, inde Moya Pete, nayenso ndi dothi? adafunsa Abiti Patuma. +Mowe Pati adangoti duu! Ngati akumangidwa madiledi. +Abale anzanga, inetu izi sindingayankhireko kanthu. Kodi si ngati zija amanena za kunena kwa ndithendithe Nanthambwe nkudzitengera. +Dr Getu Getu wa Moya Pete. +Malamulo Khumi pa Wenela Tsikulo Moya Pete adadabwitsa tonse. Adafika kumalo otsegulira msonkhano wa ana aja amalimbana za ziii! chaka ndi chaka ati kunamizira kutukula Wenela atavala ovolosi yake phiii! Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mukudabwa? Nafenso tidadabwa zedi chifukwa tsikulo lidali Lachisanu. +Kodi mesa adati tizivala miyado, nkhwende, nyanda ndi zina zotere, tsono izi za maovololo zadza ndi yani? Abiti Patuma adafunsa. +Abale anzanga inetu palibe icho ndidatolapo. +Zinthu zina zimaphweka kuyambitsa koma nzovuta kumalizitsa. Uku nkuponya sitepe imodzi kutsogolo, atatu kumbuyo, adaonjeza. +Sindikudziwa kuti izi zovala ovololo wazitengera kuti Moya Pete. +Dzulo ndachotsa uyu ndalemba uyo, dzulo ndachotsa uyu kwambiri ndalembanso wina. Ine ndi mlembi kwambiri, ndinenso mchotsi. Ndikunena pano mankhwala apezeka, misewu yochuluka ndikonza, mukanena za nyanja kwambiri, ndikuyankhani zimene ndakhala ndikunena kwa zaka 126. Amene sakudziwa akakolope nyanja kwambiri, adatero Moya Pete. +Adalankhula nthawi yaitali, mpaka enafe tidayamba kugona. +Inu mumayesa kuti ndikambapo za lamulo lakuti Paparazzi azitha kupeza zinsinsi zanga mosavuta mwauponda kwambiri. Ndingadzilume ndekha chala? Ana oipa moyo kwambiri, adapitiriza Moya Pete. +Adamwera madzi, ena adali kuliza mkonono. +Ndipo mumayesa ndinena za amene amagula mafupa a anthu a chialubino! Ngoooo! Imeneyo si nkhani kwambiri. Opezeka ndi mafupa sakumangidwa? Ndiye ndikumva zamkutu kwambiri mukuti ndizisainira kunyonga akupha anthuwa? Mumfune, adabwekera. +Adacheukira uku ndi uko. +Msewu wa Kunenekude tikonza; msewu wa Chenzi tala adutsa kuposa pa Dzaleka pamene adafika zaka 8 zapitazo. Ngati mumaganiza ndichotsa Mowe Pati chifukwa chobweretsa miyandamiyanda ya anyamata athu a Dizilo Petulo Palibe kuti ayambe kulondera pano pa Wenela mwauponda, adalankhulabe. +Adalankhula kwa maola angapo. +Zaka ndi zaka mumatitaira nthawi kunena zomwezomwezo. Manyazi ndi umunthu mudazitayira kuti? adatero Abiti Patuma. +Musataye nthawi kunena za ine mutopa chifukwa panopa ndikutuma mwana wanga womupeza akasaine zikalata zina za boma kwambiri. Mwaiwala malamulo khumi? adafunsa Moya Pete. +Sindingawaiwale mavesi amene tidaphunzira kusukulu sande: Ndine Moya Pete, amene ndidakuchotsani muukapolo wa Adona Hilida wothawa chithunzthunzi chawo. Musakhale nawo atsogoleri ena pano pa Wenela koma ine ndekha. Muzipachika chithunzi changa pamakoma a nyumba zanu. Mukhoza kugwiritsa dzina langa kuti mupatsidwe msanga kontirakiti. Muzisunga tsiku limene ine Moya Pete ndidabadwa ndi kulilemekeza. Musalemekeze makolo anu ngati ndi a Polisi Palibe kapena Male Chauvinist Pigs. Mukhoza kupha, kuchita chisembwere, kuba ndi kunamizira ena ngati mukufuna kundisangalatsa. Mukhoza kulandaa mkazi wa mwini ngati anyoza Dizilo Petulo Palibe. +Awiri afa ndi bibida ku KK Abambo awiri amwalira ndi mowa wa kachaso mnjira zofanana koma malo osiyana mboma la Nkhotakota. +Mneneri wa polisi mbomali, Williams Kaponda, wauza Msangulutso kuti Mphatso Chinguwo, wa zaka 30, adagwa nkumwalira pamalo ake ogwirira ntchito atalenguka ndi kachaso, pomwe Khiri Bwalo, wa zaka 29, adagwera mchitsime akuchokera komwa kachaso. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kutcheza kachasu: Mowawu umalengula kupanda kuudyera Nkhani zonsezi zachitikadi koma malo ake ndi nthawi nzosiyana ngakhale kuti onse adamwalira chifukwa chomwa kwambiri kachaso osadyera ndipo Chinguwo adalenguka kwambiri kaamba koti amakakamira kugwira ntchito, adatero Kaponda. +Iye adati Chinguwo amagwira ntchito yopopa mapaipi otsekeka ndi mnzake Alfred Green, wa zaka 32, mmudzi mwa Mngoma kwa T/A Mwadzama mbomali ndipo Lachinayi, ali mkati mogwira ntchitoyo iye adangogwa, osaphuphaso. +Kaponda adati mnzakeyo ataona izi adagwidwa tsembwe ndipo adathamanga kukaitana anthu ndipo adakafika naye kuchipatala atamwalira kale koma monga mwa mwambo, apolisi adapempha achipatala kuti ayese mtembowo nkuwona chomwe chidamupha ndipo adapeza kuti kudali kulenguka ndi kachaso. +Timakana kuti pazikhala maphokoso munthu ataikidwa kale poganizirana kuti mwina womwalirayo adachita kuphedwa koma zotsatira zidasonyeza kuti adamwa mowa wa kachaso wambiri osadyera kanthu ndiye adalenguka nawo, adatero Kaponda. +Iye adatiso Bwalo, wa mmudzi mwa Tchale, T/A Mwansambo, adalawira bambo ake, Gibson Bwalo, a zaka 63, kuti akukamwa kachaso ndipo pobwererako usiku wa pa 27-28 March adagwera mchitsime. +Pa 27 March adanyamuka mma 6 koloko madzulo wa kukachaso mmudzi mwawo momwemo ndipo adapezeka mchitsime mma 6 koloko mmawa wa pa 28 March. Uyuso atamuyesa, adapeza kuti adatsamwa ndi madzi mchitsime momwe adagweramo koma kadali kaamba koledzera ngati woyamba uja, adatero Kaponda. +ANATCHEZERA Wamkulu ndine Zikomo agogo, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndili ndi chibwenzi koma timasiyana ndi chaka chimodzi, wamkulu ndineyo. Kodi tingathe kukwatirana? Iyeyu akufunitsitsa atandikwatira chifukwa amandikonda kwambiri ndipo inenso ndimamukoinda zedi. +CM Lilongwe Wokondeka CM, Zikomo pondilembera. Kusiyana zaka chisakhale chopinga kuti mukwatirane, bola chikondi ndi kulemekezana. Si chifukwa mkazi kukhala wamkulu pakubadwa bola chikondi. Chimene chimavuta nthawi zina ndi kudererana mbanja, kapena kusapatsana ulemu. Pali akazi ena amene salemekeza amuna awo ati poti iwowo ndiwo ndi aakulu pobadwa, koma pachikhalidwe chathu mkazi ayenera kulemekeza mwamuna wake ngakhale akhale wochepa msinthu ndi zaka zobadwa. Chimodzimodzi mwamuna akakhala wamkulu pobadwa naye ayenera kulemekeza banja lake, osatenga mkazi wake ngati mwana chifukwa choti ndi wa zaka zocheperako kuposa iye. Mbanja laulemu mudza mwamuka akuti awa ndi akazi anga ndipo mkazi naye amati awa ndi amuna anga osati uyu ndi mkazi wanga kapena uyu ndi mwamuna wanga pagulu. Tsono ngakhale wamkulu ndiwe pobadwa umulole mwamunayo kuti mukhale thupi limodzi ngatidi pali chikondi chenicheni pakati panu. +Akukana woyera Agogo, Ndine mtsikana wa zaka 23 ndipo ndapeza mwamuna ndipo iye akuti akufuna ndimuberekere mwana koma akuti tisamange ukwati woyera. Komanso ndamva kuti anakaonetsa kale mkazi kwawo. Koma kunena zoona mwamunayu ndamukonda , nditani pamenepa? LL, Area 1, Lilongwe Wokondeka LL, Apa ndiye ukufuna ndikuuze chiyani, mwana wanga? Ukufunsa chinyezi mbafa, nanga ndinene kuti chiyani? Apa zikuonekeratu kuti mwamunayu alibe chidwi choti mukwatirane koma akuti akufuna mwana, mwana wachiyani? Ungomuberekera mwana basi, mwanayo azikachita naye chiyani ngati simukhala limodzi? Iwe mwana ulibe naye ntchito? Zachibwana basi! Ndiye ukuti umamukonda mwamunayu, chikondi chako chili pati poti iye wachita kunena yekha kuti sakufuna ukwati ndi iwe koma zogonana basi, ndipo wanena wekha kuti adakaonetsa kale mkazi wina kwawo, ndiwe iwe ukufunsa kuti utani pamenepa? Umusiye basi, upeza wina wofuna banja osati zamasanje zomwe akunena mwamunayo ayi. Kulera mwana si ntchito yapafupi, imafunika banja lachikondi ndi logwirizana. Ndiye ngati iyeyo za banja ali nazo kutali ndi iwe, chotayira ntchawi yako ndi iyeyo nchiyani? A Gama abwerere Ine ndine Mrs Jean Makolosi. Amuna anga adachoka chaka chatha kupita ku Mzuzu komwe ndamva kuti akwatira mkazi wina. Ndikufuna mwamuna wanga abwereko mwamnsanga popeza sitinayambane. Mwamuna wanga ndimamukonda, abwere mwezi uno usanathe chonde. Dzina lawo ndi a Paul makolosi Gama. +Zaka 30 zolimbana ndi umphawi zapita mmadzi Bungwe loona za maphunziro, sayansi ndi chikhalidwe mumgwirizano wa maiko a dziko lapansi la UNESCO lati dziko la Malawi lalephera kutukula miyoyo ya anthu ovutika mzaka 30 zomwe lakhala likuyesetsa kutero. +Zotsatira za kafukufuku yemwe bungweli lidapanga pogwiritsa ntchito nthambi ya zakafukufuku ya Centre for Social Research, zaonetsa kuti mmalo mosintha miyoyo ya anthu, mfundo zomwe boma lakhala likutsatira mmagawo atatu zangowonjezera mavuto a Amalawi. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndondomeko zothetsera umphawi zalephera kukwaniritsa zolinga zake pamene Amalawi ambiri akusaukirasaukirabe Zotsatira za kafukufuku yemwe adachitika, zaonetsa kuti mavuto omwe amayi, achinyamata, ana angonoangono ndi olumala amakumana nawo adaonjezereka chifukwa cha mfundo zomwe zimayenera kuchepetsa mavutowo, lipoti la zotsatira za kafukufukuyo latero. +Malingana ndi lipotili, ndondomekozi zidayamba mzaka za mma 1980 pomwe mabungwe a World Bank ndi International Monetary Fund (IMF) adayambitsa pologalamu yosintha zinthu ya Structural Adjustment Programme. +Itatha pologalamuyi, mzaka za mma 1990, boma lidakhazikitsanso pologalamu yothetsa umphawi ya Poverty Alleviation Programme, kenaka Poverty Eradication Programme ndipo itatha iyi, kudabweranso pologalamu ya Malawi Growth and Development Strategy (MGDS). +Lipoti la bungwe la UNESCO lati chodandaulitsa nchakuti mapologalamu onsewa adalephera kukwaniritsa zolinga zake koma mmalo mwake zidangoonjezera mavuto omwe zimafuna kuthetsawo. +Potsirapo ndemanga pa zomwe bungweli lanena, nduna ya zachuma Goodall Gondwe wati kutsutsa zotsatira za kafukufukuyu nkulakwitsa koma chofunika ndi kuunika momwe muli zigweru zofunika kukonza kuti mavuto a umphawi ndi kusiyana pachuma pakati pa opeza ndi osauka kuchepe. +Gondwe adati boma lipanga zotheka kuti mavutowa azitha pangonopangono mpaka idzafike nthawi yoti anthu onse ali pamtendere ndipo mavuto awo achepa. +Katswiri pa zachuma Henry Kachaje wati nkhani yotukula chuma ndi kuchepetsa mavuto omwe anthu amakumana nawo njofunika kugwirana manja pakati pa boma, makampani omwe si aboma ndi mabungwe. +Mkuluyu wati kuti chuma chikwere ndipo anthu apepukidwe, mpofunika kuyamba kutukula ntchito za malonda ndi kukonza kayendetsedwe ka chuma cha boma pokonza ndondomeko ya chuma yabwino ndi kuitsatira. +Nkhani yothetsa mavuto si yapafupi koma njotheka bola patakhala ndondomeko yabwino ya chuma cha boma ndi njira zoyendetsera ndondomekoyo mwaluntha. China ndi kulimbikitsa mgwirizano pakati pa boma, makampani ndi mabungwe, adatero Kachaje. +Aphungu a ku Nyumba ya Malamulo akuyembekezeka kuyamba mwei uno kuti akakambirane za ndondomeko ya chuma cha 2016/2017 ndipo Kachaje adati apa ndipo poyenera kuyambira popanga ndondomeko yoganizira za umphawi wa anthu. +Malinga ndi zotsatira za kafukufuku yemwe adachitikayu, mavuto monga kusiyana kwakukulu pa chuma pakati pa magulu a anthu osiyanasiyana, nyumba za boma zomwe sizidamangidwe moganizira anthu olumala ndi kusiyana mphamvu pakati pa amayi ndi abambo ndi ena mwa mavuto akuluakulu. +Lipoti la bungwe la Oxfam lomwe nyuzipepala ya The Nation ya pa 22 January, 2016, lidadzudzulanso mchitidwe wolowetsa ndale pa chuma cha dziko womwe lidati kukupangitsa kuti vuto la umphawi lizinkera mtsogolo. +Lipotilo lidati atsogoleri a ndale ndi amabizinesi akuluakulu amadzikundikira chuma pomwe anthu osauka akungosaukirabe. +Mkulu wa bungwe la Aid and Development Charity, John Makina, adati zomwe zili mulipotili zimaonekera poyera potengera nyumba ndi sitolo amakono zomwe zikumangidwa mmizinda ikuluikulu ya Lilongwe, Blantyre ndi Mzuzu. +Iye adati pomwe mmizindayi mukutukuka chonchi, mmadera akumidzi akunka nalowa pansi kusonyeza kuti ndalama zili mmanja mwa anthu ochepa pomwe ambiri akuvutika. +Mavuto ena ndi kuchepa kwa chisamaliro kwa anthu okalamba, ana amasiye ndi mabanja omwe amayanganiridwa ndi amayi kapena ana, zomwe zimapangitsa kuti anthu opempha azichuluka, makamaka mmisewu ndi mmizinda ya dziko lino. +Manambala akusonyeza kuti magawo atatu a ndondomeko zomwe takhala tikutsatira sadaphule kanthu polimbana ndi kusiyana pakati pa anthu monga amuna, amayi, asungwana ndi ana achichepere, likutero lipotilo. +Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a anthu olumala la Federation of Disability Organisations in Malawi (Fedoma), Amos Action, adati anthu olumala ndi amodzi mwa anthu omwe amakumana ndi mavuto aakulu monga kusalidwa. +Iye adati mfundo zina zomwe zidakhazikitsidwa nzabwinobwino koma vuto limakhala potsatira mfundozo kuti zotsatira zofunikazo zikwaniritsidwe. +Ntchentchefly zivuta ku Lilongwe Tsiku limenelo tidakhala pa Wenela ndipo Abiti Patuma adati tipite ku Lilongwe kumenetu ndalama zabooka malinga ndi ungano wa aphungu komanso malonda a fodya. +Adati nditsagane nawo kumeneko. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Tidaimatu pa Roundabout pa Kameza kuimitsa galimoto iyi ndi iyo. Nthawiyo nkuti Abiti Patuma atapita kukagula madzi koma atangobwera, galimoto zitatu zidatiimira. +Anti, mukupita kwa Chingeni? Tiyeni, adatero mkulu mmodzi. +Ayi ndithu, adayankha Abiti Patuma. +Inetu wa ku Mwanza, mukupita kumeneko? Kwerani ulere anthu atatu, mzimayiyo akhale kutsogolo, adateronso mkulu wina wa galimoto yake yopuma. +Abiti Patuma adapukusa mutu. Ndidagwira mchiuno, kuthodwa. +Posakhalitsa padatulukira galimoto ina yofiira. Sindinaonepo galimoto yopuma ngati imeneyo. +Tikukakhazikitsa galimotoyi ku Lilongwe. Ya madzi iyi. Mtidzi osanena. Tiyeni, adatero amene amayendetsayo. +Ndani akadakana mayesero okwera galimotoyo? Abiti Patuma adakwera kutsogolo. +Nkhani imodziimodzi zidali kuphulika. +Ndikuchokera ku Nansadi ku Thyolo. Ndaona kuti kukumangidwa nyumba zina. Mudzi uja basi ukhala tauni, Blantyre kulenga, adatero mkuluyo, tikudutsa pa Zalewa. +Apolisi adali mbweee! Koma palibe adaimika galimotoyo. +Mwati ku Thyolo kukumangidwa nyumba zina? adafunsa Abiti Patuma. +Sindinatero. Malo angopezeka kuti pamangidwenso manor ina. Mulimba? adafunsa mkuluyo. +Abale anzanga, musandifunse kuti amatanthauzanji chifukwa sindikuyankhani. Nanga kwathu kwa Kanduku ziliko izi za ma manor? Mpumulo wa Noma nawo ulipo kale. Kodi simukudziwa iyi ndi penshoni? Ndani safuna zabwino kuukalamba? adafunsa mkulu uja. +Adandipindanso. +Tsono titafika ku Lilongwe, mkulu uja adati tizungulire. +Ndisaname, tidazungulira monse adayenda anyamata aja asadaomberane kalelo. Mukuwadziwa. Aja adazungulira Lilongwe yonse akusakana, mikangano ya ziboliboli kufuna kusinthitsa ndalama kuzungulira malo onse omwera mpaka kukaomberana pachipata kulimbirana ndalama zobooka za Adona Hilida. +Koma Adona Hilida ali kuti? Kodi nsalu ija ankapachikira paphewa akupachikabe? Nanga Richie, bambo wa kwawo akupita nawo konse ayenda muja ankachitira kalelo? Tidafika ku Nyumba ya Malamulo. Tidapeza anthu akupha tulo. Inde, adali atalumidwa ndi kashembe, ntchentchefly ija yotchedwa tsetse imene imayambitsa trypanosomiasis, nthenda yogonetsa. +Tsono mkulu akupha tulo apayu, uyu Joliji, mwati akudzatenga fupa la Moya Pete? Nanga tulo take timeneti adzatithandiza? adanongona Abiti Patuma. +Mwamuiwala kodi? Pajatu ankati aletsa zotsitsa mpweya pagulu, ndidatero. +Tsono momwe mukumuonera iyeyo, akuchita emit ma gas ochuluka bwanji to bring environmental degradation or is it climate change? adafunsa Abiti Patuma. +Adandipinda. +Sindimagona ine. Ndimaphethira ine. Ine wanuwanu, amene ndidzatenge mpando wa Moya Pete sindimagona ine. Ndimaphethira ine. Mwana wanga ndi msangalatsi. mwamuiwala Izeki? Mwana wanga ankafuna kukhala ngati Izeki. Koma ineyo ndikufuna kudzakhala Moya Pete, musandiipitsire mbiri ndi za tulo, adalira munthu wamkulu. +Abiti Patuma adamupatsa sand paper. Ati chibwano kaya chatani kaya. +Omanga mvula awaothetsa moto likuswa mtengo Kudali gwiragwira Loweruka lapitalo mmidzi ya Kazembe, Golosi ndi Ntamba kwa T/A Nkalo mboma la Chiradzulu pamene anthu olusa adagwira anthu 7 ndi kuwaothetsa moto masanasana ati chifukwa chowaganizira kuti ndiwo ankamanga mvula mderalo. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Gulupu Ntamba komanso amene amaona nkhani za chitetezo kuderalo, Fanny Chinyanga, atsimikiza kuti izi zidachitikadi koma ngakhale apolisi adadziwitsidwa palibe amene wamangidwa. +Koma mneneri wapolisi mboma la Chiradzulu, Victoria Chirwa, adati sakudziwapo chilichonse pa nkhani ya kuzunzidwa kwa anthu 7 ndipo adati apolisi afufuza. +Mwa anthuwo, atatu ndi okalamba pamene mtsikana adalipo mmodzi. Atatu enawo adali abambo. +Chinyanga akuti izi zidachitika masana dzuwa likuswa mtengo pamene anthuwo adagwidwa ulendo nawo kubwalo la mmudzi mwa Ntamba komwe adawakolezera moto kuti aothe. +Poyamba adagwira okalambawo ndipo adayamba kuululana ndiye amene amatchulidwawo kuti ndiwo akutseka nawo mvula amawagwira ulendo nawo ku bwaloko. +Anthuwa adawasiya atatsimikizira gululo kuti mvula ibwera mmawa wake. Ndipo kudagwadi mvula yambiri tsiku limenelo, adatero Chinyanga amene wati kuderalo mvula idasiya mu January. +Iye wati izi zitayamba kuchitika, achitetezo amderalo adadziwitsa apolisi ya Nkalo koma mpaka pamene anthuwo amamasulidwa, apolisi sadabwere. +Komabe poti ife ndi achitetezo cha mmudzi, tikufufuza nkhaniyi ndipo tikawagwira amene adazuza anthuwa ndiye tiwapititsa kupolisi. +Koma mneneri kunthambi ya zanyengo Elina Kululanga wati ndi kulakwa kuzuza anthu chifukwa cha vuto la mvula ponena kuti palibe amene angamange kapena kutsekula mvula. +Mawu a Kululanga akudzanso pamene miyezi iwiri yapitayo, okalamba anayi adaphedwa kwa Dambe mboma la Neno kuti adalenga mphenzi yomwe idapha mtsikana wa zaka 17. +Izi nzachikale ndipo dziwani kuti palibe munthu angamange kapena kugwetsa mvula. Ngakhale mphenzi silengedwa ndi munthu, koma anthu amaona ngati izi zingatheke. +Chaka chino mvula yavuta madera ambiri, kotero anthu asaganize kuti alipo amene akukhudzidwa ndi kuvuta kwa mvulaku, adatero Kululanga, amene adalangiza anthuwa kuti azimvera zanyengo pawailesi kapena kudzera mnyuzipepala. +Sabata yathayi takhala tikulosera kuti mvula sibwera ndipo tidanenanso kuti sabata ino kuti chigawo cha kummwera chilandira mvula yambiri ndipo mwaonanso zikuchitika, ndiye anthu azimvera zomwe tikunena. +Gulupu Ntamba wati panthawi yomwe izi zimachitika, iye nkuti ali mnyumba ndipo sangathe kufotokoza zomwepo kanthu. +Oferedwa akusowa mtendere ku ntchisi Adanena mawu oti mvula ikakuona litsiro sikata sadaname. Banja la anamfedwa ena ku Ntchisi likusowa mtendere pamene nyakwawa ya mmudzi mwawo yauza banjalo kuti lichitepo kanthu pa imfa ya ana awo zitamveka kuti ana omwalirawo auka ndipo akumagogoda mmakomo mwa anthu. +Koma banja loferedwali lati silikudziwa choti lingachite ndi zomwe zikulankhulidwazo. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mphenzi ngati iyi ndi yachilengedwe koma ena amaganiza kuti ena amatha kulenga mwamatsenga Tate wa anawo, Samson Mvula, wa mmudzi mwa Chungamiro kwa T/A Malenga mbomalo wati anawo adafa mwangozi pa 17 February chaka chino pamene mphenzi idaomba nyumba yawo. +Iye adati usiku wa ngoziwo iye ndi ana ake anayi adagona pabalaza ndipo mwadzidzidzi kudamveka chiphaliwali chomwe chidakuntha nyumba yawo ndipo mnyumba monse mudadzadza utsi kuti kobo! Adali madzulo cha mma 7 koloko. Ine ndi ana onse tidagona pabalaza. Wamkulu adali wa zaka 15, wina 14, 9 ndi womaliza wa zaka zisanu. +Mphenzi idaomba mvula itangoyamba kumene. Idamenya pabalazapo ndipo mnyumba monse kudzadza utsi. Ine ndi mkazi wanga tidayamba kutulutsa anawo amene adali atafookeratu. Tidathamangira nawo kuchipatala, koma zachisoni, wa zaka 14 ndi 9 adamwalira, enawo adatsitsimuka ndipo ali moyo, adatero Mvula. +Pa 18 February mudzi udasonkhana kuwaperekeza anawo kumanda, koma akuti zodabwitsa zidayamba kuoneka. +Mvula adati ali kumandako, anthu ena akuti adayamba kuwaona anawo akuyendayenda maliro ali mkati. +Adandifunsa ngati ndingakwanitse kuwaona anawo. Ndidawauza kuti ine sindidatemere ndiye sindingakwanitse. Koma amene adatemera ndipo angathe kuona zaufiti amati anawo akuwaona, adatero Mvula. +Patangotha sabata, akuti mphekesera zidayamba kumveka kuti anthu ena ayamba kukumana ndi anawo. Mmodzi mwa anthuwo ndi nyakwawa Chungamiro yemwe wauza Msangulutso kuti anawo adafika kawiri kunyumba kwake. +Afika kawiri koma usiku okhaokha, ndidamva mapazi komanso akumagogoda akafika pakhomo, poti ndituluke uona akuthawa, adatero Chungamiro. +Titafunsa nyakwawayo kuti idadziwa bwanji kuti ndi ana omwe adafa amene ankagogoda pakhomo pakeusiku nkuthawa? Idayankha: Kunena zoona sindidawaone, koma ena amene adakumana ndi anawo masana ndi amene awazindikira. Ndiye chifukwa akumayenda mmakomo kumagogoda, tikungoganiza kuti ndi iwowo amene akuchita izi. +Mfumuyi yati yalandira madandaulowa kwa anthu oposa 7 ndipo idaitanitsa banja loferedwali Lolemba sabaya yatha kuti iwauze chochita. +Ndawauza kuti apeze njira kuti mizimu ya anawo igone pansi. Apeza njira, mwina akudziwa chomwe chikuchitika, idatero mfumuyo, yomwe sidafotokoze njira zake. +Koma tate wa anawa wati nayenso ndi wodabwa kuti amfumuwo amuuza kuti achitepo kanthu pamene iwo sakudziwapo kalikonse za zomwe zikuchitikazo. +Anthu akungolankhula kuti akumana ndi ana anga koma inenso ndikusowa kuti ndivomereza bwanji chifukwa sindidawaone ngakhale anthu akulankhula choncho. Izi zikutisowetsa mtendere ndipo tikulephera kuiwala mavuto adatero Mvula. +Ndikulira ine, ndiye ndilibe mphamvu kuti ndiletse izi. Iwo akuti ndipondeponde koma ndilibe ndalama zopangira zimenezo chifukwa ndalama zanga zidatha panthawi ya zovutazi, adatero tateyo. +Koma mfumuyi yati anthu akuchita mantha ndi nkhani zikumvekazo nchifukwa chake idaganiza zoitanitsa banjali kuti lichitepo kanthu. +Olowa mdziko mozemba aonjeza mavuto mndende Mavuto a mndende za mdziko muno ngosakamba koma kafukufuku wa Tamvani wasonyeza kuti ena mwa mavutowa akudza kaamba ka anthu osamangidwa koma ongosungidwa mndende chifukwa cholowa mdziko muno popanda chilolezo. +Malingana ndi wachiwiri wa mneneri wa nthambi yoona za anthu olowa ndi kutuluka mdziko muno, Wellington Chiponde, chiwerengero cha anthu oterewa chimasinthasintha kaamba koti yemwe wakonzeka amatuluka nkumanka kwawo. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ena mwa olowa mdziko muno popanda chilolezo atawagwira ku Nkhata Bay Aliyense mwa anthuwa amadzionera yekha chochita kuti abwerere kwawo, chifukwa boma siliperekapo chilichonse kupatula kuwadyetsa ndi kuwasunga pamalo okhazikika, omwe nkundendeko, adatero Chiponde. +Iye adati anthuwa sakhala kundendeko ngati akayidi koma ngati njira yowathandizira malo okhala ndi chakudya poyembekezera kuti azipita kwawo akakonzeka polingalira kuti dziko lino lilibe malo osungirako nzika za maiko ena zolowa mdziko muno popanda chilolezo. +Chiponde adati malamulo amalola anthu oterewa kusungidwa mndende kwa sabata ziwiri zokha ndipo ikakwana nthawiyi amafunsidwa ngati apeza njira yopitira kwawo, koma ngati njirayo sidapezeke, amawapatsanso masiku ena kufikira pomwe adzakonzeke kubwerera kwawo. +Si nkhanza, ayi, koma malamulo a dziko amatero kuti nzika ya dziko lina si yoyenera kukhala mdziko muno popanda chilolezo pazifukwa zingapo. Mudziwa kuti boma limayenera kupanga ndondomeko ya zinthu zambiri monga chitetezo, mankhwala, chakudya ndi zina. +Kuti ndondomeko imeneyi iyende bwino, boma limayenera kudziwa chiwerengero cha anthu omwe ali mdziko nchifukwa chake othawa nkhondo kapena odzausa mwandondomeko amakhala ndi zowayenereza ndipo amakhala ndi malo awoawo, adatero Chiponde. +Iye adati malamulo oterewa ali mdziko lililonse ndipo maiko ena ali ndi malo akeake osungirako anthu oterewa koma poti dziko lino likadalibe malowa, limasunga anthuwa mndende. +Potsirapo ndemanga pankhaniyi, mneneri wa zandende mdziko muno, Smart Maliro, adati ichi nchipsinjo chachikulu kwa akuluakulu oyanganira za ndende polingalira kuti iwo amayenera kuti azidyetsa ndi kuyanganira anthuwa kufikira pomwe adzatuluke. +Naye adati chiwerengero cha anthuwa chimasinthasintha kutengera ndi momwe akulowera komanso kutuluka koma zonse zimatengera kuti a nthambi yoona za anthu olowa nkutuluka anenanji. +Ife timangolandira nkusunga anthuwa koma zonse amayendetsa ndi anthambi yoona za anthu olowa nkutuluka mdziko chifukwa sikuti anthuwa ndi omangidwa, ayi. Nkhawa yathu imangokhala pachisamaliro chifukwa zonse zimagwera ife. +Mwachitsanzo timayenera kupeza malo oti akhalepo, chakudya komanso poti chiwerengero cha anthu mndende chimakwera, zinthu monga madzi ndi zina zimagwira ntchito kwambiri ndiye mabilu nawo amakwera, adatero Maliro. +Nawo oyanganira za maufulu a anthu ati zomwe amaona anthu olowa mdziko mwachinyengowa nzopweteka komanso zowaphwanyira ufulu kaamba koti amasungidwa mmalo oyenera omangidwa. +Mkulu wa bungwe la Centre for Human Right and Rehabilitation (CHRR), Timothy Mtambo, adati ndende za mdziko muno zili ndi mbiri zosakhala bwino, makamaka pankhani yothithikana, zaumoyo ndi kuvuta kwa chakudya. +Mkuluyu adaona kuti kusunga anthuwa mmalo ngati amenewa nkuwalakwira kwambiri potengera malamulo a zaufulu wa anthu padziko lonse. +Kumeneko nkulakwa chifukwa anthuwa sadamangidwe, ayi, akungoyenera kutumizidwa kwawo basi osati mpaka kumasungidwa mndende ngati kuti azengedwa mlandu nkumangidwa, adatero Mtambo. +Iye adati njira yabwino nkumanga malo osungirako anthu oterewa poyembekeza kuti azinka kwawo monga momwe zilili mmaiko ena. +Nduna ya zamdziko, Jappie Mhango, adati ganizo lomanga malo osungilako anthuwa ndi labwino, makamaka pankhani yachitetezo, koma adati pakalipano palibe mapulani otere polingalira mavuto a zachuma omwe ali mdziko muno. +Ndi maganizo abwino kwambiri chifukwa anthuwa amachokera kosiyanasiyana ndiye sitinganeneretu kuti moyo wawo ndi wotani. Mwina ena adali zigawenga zikuluzikulu kwawo, akhoza kuphunzitsa anthu anthu omwe ali mndende, adatero Mhango. +Iye adati mtsogolo muno zinthu zikadzayamba kuyenda bwino, boma lidzaganizirapo kuti mwina lidzamange malo osungirako anthuwa kuti azikakhala kwaokha. +Za Jessica Bwira ndi zina Mvula idagwa tsikulo pa Wenela si ndiyo. Kaya inkachokera kuti kaya! Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Abale anzanga, musandifunse za Jessica Bwira, Mwano Mkangama komanso Pierre Chamkhwatha. Zoziyamba dala! Kodi mwati foni ingalande ufumu wa Mose? Zidaliko pa Wenela tsikulo. +Inetu za WhatsApp ndi zina zotero ndilibe nazo gawo. Komabe ndikudabwa kuti asirikali awa pa Wenela adayamba liti kulowetsa anthu kozizira pofuna kuwachenjeza. Zachilendo ndithu, adatero Abiti Patuma. +Ukungonena iwe. Kuchezatu kwaphweka ndipo kwatchipa. Kunena zoona, ngakhale Male Chauvinist Pigs akudziwa bwino lomwe kuti ana a Farao adagwiritsa ntchito kwambiri foni kuthamangitsa Farao ku ma pyramid a ku Gizeh. Umamudziwa Cheops iwe? Nanga chidathyola mphuno ya The Great Sphinx nchiyani? Sindikukambatu za Great Sphinx of Quartz, adatero mkulu adali naye tsiku limenelo. +Kaya ndi sukulu kaya ndi chiyani koma sindikudziwa kuti ankakamba chiyani. Iye ankalankhula mokuluwika ngati Moya Pete. +Zonse zili apo, apatu zangosonyezeratu kuti ku Male Chauvinist Pigs kuli amthirakuwiri. Nanga achina Niko adziwa bwanji izo amakambirana kuchipinda cha foni? adafunsa Abiti Patuma. +Zoona. Koma mpaka kuwamanga kuti awachenjeze? Chadza ndi yani? adafunsa mkulu uja. +Nkhani imene idatifika pa Wenela idali ya kutengedwa kwa Jessica, Mwano ndi Pierre. Iyitu ndiyo nkhani idaphimba za mneneri Bushi Minor amene waletsedwa kugawa nandolo ndi chipere chifukwa Moya Pete wakhuta kwambiri ndipo sakumvanso njala. Sakufunanso kumva zakuti wina wagona ndi njala. +Koma ndiye zinaliko! Khoba ngazingazi kuchita zawo zija pa Lilongwe apa! Mumayesa masewera? adailowa nkhani Gervazzio. +Kodi Moya Pete simesa adatiuza kuti zomangana za ziii pano pa Wenela ayi? Nanga apa alonda ake akuti chiyani? adafunsa mkulu adali ndi Abiti Patuma. +Adakuuzani zomangana zokhazo? Musaiwaletu kuti adabweretsa ana ake aja kuti mukhulupirire kuti iyeyo sadagwe mumtengo wa papaya. Lero anawo angabwerenso pano pa Wenela kuti adzafe ndi njala ngati gogo uja? adafunsa Abiti Patuma. +Langatu lidali khutu chabe. Mlomo wanga udali womangidwa ndi loko ngati sefa ya ku Reserve Bank. +Ndiye ndikumva kuti mayi wathu amupatsa tsamba lapamwamba, unganga wodziwa kusesa ndi kukolopa zimbudzi, adaisintha nkhani Abiti Patuma. +Simukudziwa inu. Pamene mukubwebweta za njala simukudziwa kuti iyi ndi njira yothetsera phokosolo? Zinyalala momwe zachulukira pano pa Wenela wina nkumalandira nazo masamba? Koma abale, misalatu yachuluka pano pa Wenela, adatero mkulu uja. +Abale anzanga, musandifunse za zinyalala pano pa Wenela. Nokha simukuona? Fungo lochoka mumtsinje wa Mudi silitseka mfuno zanu? Mfemvundikunena mphemvusizinaberekane phwamwamwa pano pa Wenela? Tsono ngati akulandira tsambali, amene amasesa mumsewu awapatsa chiyani? adafunsa Abiti Patuma. +Pamene mukuti kuli njala, simunamve kuti tikutseguliranso msewu uja adatsegulira Adona Hilida? Simudamve tikutseguliranso msewu uja adausintha dzina Mpando Wamkulu? Zochita kuphiri ziliko zambiri. Zikuyenda pa Wenela, adatero mkulu uja, uku akuvula malaya ake kuti ationetse T-shirt yake ya mtundu wa thambo pali zitsononkho zitatu. +Chenjezo: Makolo a ana opemphetsa azinjatidwa Apolisi mumzinda wa Blantyre ati nthawi yatha ndipo tsopano ayamba kumanga makolo a ana amene apezeke akuyendayenda nkumapemphetsa mmisewu ya mzindawu. +Mkulu woyanganira mgwirizano wa apolisi ndi anthu papolisi ya Blantyre, Horace Chabuka, adanena izi masiku apitawa pasukulu ya Mbayani pomwe apolisi ndi bungwe loona za ufulu wa ana la Chisomo Childrens Club amalangiza makolo zomwe malamulo amanena pankhaniyi. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Takhala tikulekerera izi kwa nthawi yaitali koma tsopano lamulo ligwira ntchito. Nzachisoni kuti ambiri mwa ana opemphetsa mumzinda wa Blantyre amachokera kuno ku Mbayani. Izi zikuchitika chifukwa ena amatumidwa ndi makolo awo kukapemphetsa komanso makolo ena salabadira za ana awo. +Tsiku lina apolisi tidalowa mchipinda choonetsera filimu 2 koloko mbandakucha ndipo ambiri adali ana kwambiri, adatero Chabuka. +Iye adati ana opemphetsa ena amagwiritsidwa ntchito ndi achifwamba komanso akadzakula amakhala mbanda basi chifukwa sukulu imawalaka. +Malinga ndi mkulu wa Chisomo Childrens Club mumzinda wa Blantyre, Auspicious Ndamuwa, gawo lachitatu la malamulo otetezera ana limanenetsa kuti ndi udindo wa kholo lililonse kusamalira ana ake. Iye adati ndi udindo wa kholo kupatsa ana zakudya, zovala, pogona komanso kuonetsetsa kuti sakuchitiridwa nkhanza kapena kuponderezedwa kulikonse. +Malinga ndi iye, Lachiwiri likudzali ndi tsiku lokumbukira ana opezeka mmisewu ndipo, mogwirizana ndi mabungwe a Samaritan Trust komanso Step Kids Awareness (Steka), akonza zochitika mumzinda wa Blantyre zomwe mwa zina adzalangize anthu mumzindawu za lamulo lokhudza ana opemphetsa. +Izi zili apo, msabatayi nduna yoona za kuti pasakhale kusiyana pantchito pakati pa abambo ndi amayi, Patricia Kaliati adakana pempho la opemphetsa ena amene amati kuletsa anthu kuwathandiza kwachititsa kuti mavuto awo akule. Malinga ndi opemphetsawo, pomwe boma lidaletsa anthu kuthandiza opemphetsa, zawo zinada ndipo adapempha kuti boma liziwapatsa K50 000 pamwezi. +Koma Kaliati adakana pempholo, nati: Nzosatheka zimenezo. +Kucheza ndi Ibu Mphanje: Gaba wochemerera Bullets Anthu otsata masewero a mpira wa miyendo alipo ambiri koma ena amaonjeza kukonda kwake. Ena adachita kufika popereka maina achilendo kumatimu omwe amachemerera ati pofuna kuwopseza anzawo. Ibu Mpanje ndi mmodzi mwa ochemerera timu ya Big Bullets yomwe eni ake amati Timu ya Fuko kapena Ma Palestina. Ndidacheza naye motere: Mphanje: Masapota tionjezera mphamvu Moni wawa komanso ndikudziweni? Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ine ndine Ibu Mpanje kwathu nku Nathenje koma ndikukhala mtauni ya Lilongwe. Ndimakonda kwambiri masewero a mpira wa miyendo moti timu yanga ndi Big Bullets. Anthu ambiri amandidziwa ndi dzina lakuti Gabadinho, osati osewera mpira uja, ayi, koma wochemerera. +Tsono dzina la Gabadinho lidabwera bwanji? Basi kumpira anthu ambiri amandipatsa ulemu pa nkhani yochemerera ndiye nthawi ija kudadzatulukira Gabadinho wa mpira ija anthu amatengera momwe adagwedezera iye nkumandiitana ndi dzina lomwelo. +Anthu ambiritu amakonda kudzitcha okha maina a anthu otchuka, sizili choncho ndi iwe? Ayi, nokhaso mudaona momwe zidalili kuja kokhala anthu ochemerera momwe ndidagwedezera ochemerera matimu ena omwe samafunira Bullets zabwino. Zimakhala mommuja nthawi zonse kukakhala mpira, makamaka wa Big Bullets, timu yanga kuyambira kalekale. +Umangokonda mpira basi kapena uli ndi mbiri iliyonse pamasewerowa? Mpira ndinkasewera kalekale kuyambira kupulayimale mpaka mmakalabu ena ndi ena moti kusiya ndidasiyira pa timu ya KIA. Ndasewerako malo osiyanasiyana mgalaundi koma malo omwe ndidasewera kwambiri ndi kutsogolo. Kuvulala ndiko kudandichititsa kuti ndisiye kusewera mpira. Ndidavulala kamodzi ndiye kuyambira pomwepo ndinkati ndikasewera mpira ndimadzutsa vutolo. +Malingaliro ako adali otani panthawiyo? Panthawiyo ndinkafunitsitsa kudzasewera mmatimu akuluakulu makamaka ya Big Bullets moti sindikaika kuti chipanda kuvulalako, nkadafika pomwe ndimafunapo. Anthu omwe adandionererako nthawi imeneyo akhoza kufotokoza bwino za luso lomwe ndidali nalo moti pano ndimadandaula kwambiri chifukwa ndidasiya mpira ndisadasewereko mutimu ya Flames. +Chifundo chosechi pa timu ya Bullets bwanji supikisana nawo pamaudindo kuti uzitumikira nawo? Ayi, zinthu zimafunika kupatsana mpata. Ngati pali ena omwe aonetsa kale mtima wofuna kutumikira, ena mumafunika kuthandiza amenewo kuti pakhale umodzi chifukwa nonse mukamalimbirana, mkangano suchedwa kuyamba, ayi. +Sabata yathayi mwasewera masewero awiri omwe simudapambaneko. Zikutanthauzanji kwa iwe ngati wochemerera? Poti awo adali masewero ongopimana mphamvu ndiye sindingazitengere kwenikweni, koma tikudikira ligi ikayamba ndiye anthu adzaone Bullets yeniyeni. Mudaona nokha ligi yathayo momwe Bullets idavutira, chaka chino tiposa pamenepo ndipo ifenso ochemerera tionjezera mphamvu kuti anyamata osewera nawo adzadzipereke kotheratu. +Aotcha mwana chifukwa cha mkute Pamene nkhani za njala zikuyala nthenje, mayi wina ku Neno wa zaka 28 zakubadwa waotcha mwana wake mmanja chifukwa anadya mkute osapempha mayiyo. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mwanayo kuonetsa manja adatenthedwawo Mkulu wapolisi ya Zalewa, Bravo Chiperesa wati mayiyo amusiya atamulangiza kuipa kochitira ana nkhanza chifukwa banja la mayiyo lidatha ndipo ali ndi ana atatu amene akadavutika akapitiriza kumuzenga milandu. +Malinga ndi Chiperesa, mayiyo, Sophia Dankeni, amamuganizira kuti adafumbatitsa mwanayo makala a moto mmanja ngati chilango atadya mkute omwe mayiyo anasunga kuti mwanayo ndi abale ake adye nthawi ina koma iye anadya yekha kaamba ka njala. +Anthu ena a chifundo ndiwo adatengera mwanayo kupolisi koma titaona kukula kwa mabalawo tidati apite kaye kuchipatala ndipo tidadikira kuti tione zikhala bwanji, adatero iye. +Anthu ena amene analipo panthawi yomwe mwanayu amatengeredwa kupolisi adali okwiya kwambiri ndizomwe mayiyu adapanga ponena kuti njala si chinthu chokwanira kuti mayiyu akaotchere mwana wake. +Joyce Mhango: Nyale ya zisudzo Azisudzo mMalawi muno akhala akulimbika kutukula lusoli koma chifukwa cha zovuta zina ndi zina mwayi woonekera nkulandira mphotho pa zochita zawo sumapezeka. Ena adayamba kutaya mtima kuti Malawi ingapange zisudzo zoti maiko ena nkutamanda. Izi zili choncho, masiku apitawa, mmodzi mwa ochita zisudzo mMalawi muno, Joyce Mhango, adalandira chikho cha ulemu pa ochita zisudzo a mmaiko osiyanasiyana a mu Africa. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye pa nkhani yabwinoyi. +Poyamba tafotokoza kuti ndiwe ndani? Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kusonyeza chikho chake: Chavula-Mhango Ndine Joyce Mhango Chavula wochokera ku Rumphi. Ndidasankha kukhala wa zisudzo mmoyo mwanga. Makamaka ndimapanga mafilimu, kuchita zisudzo, kukhala mkonzi wa zisudzo komanso ndimayendetsa kampani ya zisudzo ya Rising Choreos. +Posachedwapa udalandira chikho kukuyamika pa ntchito yako makamaka chifukwa cha filimu yako yotchedwa Lilongwe. Amalawi ambiri ndiwonyadira chifukwa cha nkhaniyo koma sadziwa kuti filimuyi ndiyotani. Ungawafotokozere? Zoonadi ambiri mwina sakuidziwa bwino filimuyi. Lilongwe ndi filimu yomwe imakamba za mtsikana oyendayenda yemwe ali ndi ana atatu omwe adapatsidwa ndi amuna osiyanasiyana. Iye ali pantchito yabwino koma amapeza ndalama zambiri kuchoka kwa amuna okwatira omwe amagona nawo. Pambuyo pa zaka 7 kale lake la Lilongwe lidayamba kumuweruza ndipo mufilimu yonse samaiwala mawu oti Musandiweruze chifukwa simukudziwa komwe ndachokera. +Bwanji sitidamveko kuti wakhazikitsa filimi imeneyi mdziko muno? Idakhazikitsidwa mu October chaka chatha ku Lilongwe ku Cinema koma anthu ambiri adasemphana nayo. Mapulani okhazikitsanso alipo mu April chaka chino kuti anthu adzayionerere ndipo chimbale chake chifika pamsika posachedwapa. +Udalandira ulemu waukulutu koma ukuona ngati chinsinsi chake chagona pati? Ndiyambe ndi kunena kuti ndine wodala kukhala mmodzi mwa olandira ulemu umenewu. Ndidapereka filimuyi kwa woyendetsa mwambo kuti ipikisane nawo ndi mafilimu ena ndipo mwa mwayi idasankhidwa kukhala nawo mgulu la mafilimu omwe adasankhidwa. Ndimakhulupilira kuti kulimba mtima kwanga ndiko kudandithandiza pamphepete pa madalitso a Mulungu. +Zidakutengera nthawi yaitali bwanji kupanga filimuyi ndipo udakumana ndi zokhoma zanji? Zidatitengera masiku 12 ojambula mosadukiza koma kuti zonse zitheke padatenga nthawi yaitali. Nthawi yovuta kwambiri idali yokonzekera; kusankha anthu oyenera, kusonkhanitsa zofunika ndingoti padalibe kugona. Komabe zonsezo zidapita poti filimuyi yalandirako zikho ziwiri tsopano. Choyamba cha ochita zisudzo mwapamwamba ku Shunaffoz ku Zambia mchaka cha 2015 ndi ichi chapompanochi. +Amalawi valani dzilimbeMutharika Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika dzulo watsegulira nkhumano ya aphungu a Nyumba ya Malamulo yokambirana ndondomeko ya chuma choyendetsera boma kuyambira chaka chino mpaka cha mawa mmene ati muli mfundo zokhwima zomwe zithandize kutukula dziko lino, makamaka pantchito zaulimi, mtengatenga, migodi ndi zokopa alendo. +Mutharika adati ngakhale boma lidalephera kukwaniritsa zina mwa zomwe zidali mundondomeko ya chuma ya 2015/2016 kaamba ka zovuta zina, monga ngozi zogwa mwadzidzidzi, ndondomeko yomwe aphungu akambirane pano ikhala yakupsa. +Peter Mutharika Ndondomeko ya chaka chatha idakumana ndi zovuta zambiri monga madzi osefukira ndi mvula ya njomba kaamba ka kusintha kwa nyengo ndipo izi zidasokoneza ntchito zambiri, adatero Mutharika. +Mfundo zina zomwe Mutharika adakambapo ndi kupitiriza pologalamu ya zipangizo zaulimi zotsika mtengo ya sabuside yomwe adati chaka chatha idapindulira anthu 1.5 miliyoni. +Iye adatiso ndondomekoyi ipitiriza kupititsa patsogolo ntchito za ulimi wamthirira pofuna kuonjezera zokolola zomwe alimi amapeza paulimi wodalira mvula. +Ntchito zamthirira zipitirira. Monga mudziwa, nthitozi zidayamba kale mmadera monga kuchigwa cha Shire ndi madera ena kudzera mndondomeko ya Green Belt Initiative, adatero Mutharika. +Iye adati mwa zina boma lidagula ma treadle pump 4 000 othandizira alimi mmadera osiyanasiyana kuti ntchitoyi ipitilire ndi kubereka zipatso. +Mtsogoleriyu adatiso polingalira kuti chaka chino kuli njala, boma lidapereka kale ndalama kubungwe la Admarc kuti ligule chimanga alimi akakolola komanso kunja kwa dziko lino. +Pa zamtengatenga, Mutharika adati ndondomekoyi ipitiriza ntchito yomanga ndi kukonza misewu mzigawo zosiyanasiyana komanso ilimbikitsa ubale ndi maiko oyandikana nawo monga Mozambique ndi Zambia kuti agwirizane zotsegula doko la Nsanje. +Patchito zokopa alendo, Mutharika adati nthambi ya zokopa alendo ndi nthambi yomwe ingathandize kutukula dziko lino ngati Amalawi eni ake angakhale oyamba kutukula ntchitozi. +Iye adatinso ndondomekoyi ilimbikitsa kupititsa patsogolo ntchito za migodi pofuna kuonetsetsa kuti dziko lino likupindula nawo pantchitozi. +Ndondomekoyi akuti ipititsanso patsogolo ntchito za malonda polimbikitsa kukopa makampani akunja ndi a mdziko mommuno kutsegula mafakitale ndi mabizinesi osiyanasiyana. Iye adatiso akhazikitsa komiti ya anthu 200 oti afufuze chomwe chidayambitsa mchitidwe wopha ndi kuzunza maalubino, mchitidwe womwe wafika poipitsitsa mdziko muno. +Ati boma lisabweze ndalama ku FDH Anthu ena otsata mmene zinthu zikuyendera mdziko muno aopseza kuti akonza zionetsero ngati boma limvere zonena za banki ya FDH kuti libwezeko K1.1 biliyoni mwa ndalama K9.5 biliyoni zomwe adagulitsira banki ya Malawi Savings Bank (MSB). +Sabata yatha zidadziwika kuti banki ya FDH yalembera boma kuti libweze ndalamazi ponena kuti padali zingapo zomwe sadaunikire bwino panthawi yogulitsanayo. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Koma boma lakana kale kuti silibweza ndalamazo, zomwenso zasangalatsa othirira ndemanga kuti ndalamazi zisaperekedwe. +Mkulu wa bungwe lomenyera ufulu wa ogula la Consumers Association of Malawi (CAMA) John Kapito wati boma lichite zomwe likulankhula. +Zimatere kuti lero akutiuza kuti sabweza ndalamazo pamene kuseri apanga kale, tazionapo zotere zikuchitika. Pogulitsa bankiyi ife timati sagulitsa atatitsimikizira kuti satero koma mapeto ake tidamva kuti agulitsa. +Lero boma litha kutilimbitsa mtima kuti sabweza ndalamazo koma mawa mumva kuti abweza kale. Ife tikupempha kuti chonde boma lisatero, adatero Kapito. +Iye adati boma liganizire kuti zinthu sizili bwino mdziko muno kumbali ya chuma ndipo ndi kulakwa kuti ndalama zipite mnjira zotere. +Panopa tili pantchito yopeza ma triliyoni a bajeti ya dziko lino. Ndiye ngati tingapereke ndalamazi anthu akhala pamavuto chifukwa iyi ndi misonkho yathu, adaonjeza Kapito. +Mu July 2015, boma lidagulitsa MSB ngakhale Amalawi ambiri adachenjeza kuti lisagulitse bankiyi. Koma mathero ake, boma lidagulitsabe bankiyi pamtengo wa K9.5 biliyoni. +Winanso womenyera ufulu wachibadwidwe, Martha Kwataine, wati zomwe zikuchitikazi ndi kubera Amalawi ndipo boma lisayerekeze. +Banki idagulitsidwa pamtengo wotsika ndi kale, lero akuti tibwezenso ndalama zina, zoona? Ichitu nchibwana ndipo Amalawi tisalole zimenezi. Ngati boma libweze ndalamazi kumbali ife osadziwa, ndiye timema Amalawi kuti tichite zionetsero chifukwa uku nkutitengera pamgongo, adatero Kwataine. +Mayi amwalira kokafuna golide Mayi wa zaka 36 wamwalira ku Salima pamene dothi la mumtapo wa golide yemwe amafunafuna litamugwera iye ndi mwamuna wake. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mneneri wa apolisi ku Salima Gift Chitowe watsimikiza za nkhaniyi pouza Msangulutso Lolemba lapitali kuti nkhaniyi idachitika pa 8 January chaka chino pamene mayi womwalirayu, Elinati Mkaundu, pamodzi ndi mwamuna wake adanyamuka kumudzi kwawo kupita kumudzi wa Sadzu komwe ankafuna kukayesera mwayi wawo kokafuna miyala yamtengo wapatali yotchedwa galanayiti. +Chitowe adati atafika kumalo komwe kunali mtapoko mayiyo ndi mwamuna wake adafikira kulowa mdzenje la mtapolo ndi kuyamba kufunafuna miyala ija koma mwatsoka dothi lomwe lidali mudzenjemo lidawagwera ndipo mayiyu adamwalira pomwepo pamene mwamuna wake adavulala thupi lonse ponyukanyuka. +Agwiririra ndi kupha gogo Pomwe dziko lapansi likukumbukira tsiku la amayi pamutu woti Kuthetsa Nkhanza kwa Amayi ndi Ana, anthu achiwembu ku Mchinji adagwiririra ndi kupha gogo Vigilita Sakala, wa zaka 61, nkumutaya mmphepete mwa munda wake. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mneneri wa polisi mbomalo, Moses Nyirenda, watsimikiza za nkhaniyi koma wati anthu omwe adachita chiwembucho sadapezeke mpaka lero kuchoka pa 11 Mrch pomwe mtembo wa gogoyu udapezeka. +Gogoyo ndi wa ku Chipata mdziko la Zambia, mmudzi mwa Tambala, koma adakwatirana ndi mwamuna wa ku Malawi Alubano Aaron Mbewe, wa zaka 63, wa mmudzi mwa Kapita, T/A Mlonyeni ndipo amakhala mmalire a Zambia ndi Malawi, adatero Nyirenda. +Mbewe adati wakhala pabanja ndi mayiyo kuyambira mchaka cha 1976 mosangalala ndipo mkazi wakeyo ankatha kupita kwawo kukaona anthu nkubwerera popanda chovuta chilichonse kupatula patsikulo. +Pa 10 March chaka chomwe chino adatsanzika kuti akupita kwawo kukatenga nkhuni koma sadabwerere mpaka tsiku lotsatiraro pa 11 March pomwe tidayamba kuda nkhawa, adatero Mbewe. +Nyirenda adati mwana wa mnyumbamo adayamba kuyangana mayi akewo pa 11 pomwepo ndipo mma 6 koloko madzulo adapeza mayi ake atagona chagada ali mbulanda mkanjira mmphepete mwa munda wawo koma akuoneka kuti zamoyo palibe. +Apolisi atapita pamalopo adapezadi mayiyo ali momwe mwanayo adafotokozera ndipo atatengera thupilo kuchipatala, adatsimikiza kuti malemuyo adgwiriridwa ndipo adafa kaamba kobanika achiwembuwo atamufinya pakhosi, adatero Nyirenda. +Nduna yoona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa amuna ndi amayi, ana ndi okalamba Patricia Kaliati adadzudzula nkhanza zomwe gogoyo adachitiridwa ndipo wapempha apolisi kuti ayesetse kufufuza ndi kupeza omwe adachita chipongwecho. +Kuweta ngombe zamkaka nkokoma, koma. +Alimi ndi akadaulo ena pa zaulimi abwekera ubwino ndi phindu la ulimi wa ngombe, koma ati pali zina zoyenera kuchita kuti ulimiwu ufikepo. Mwa zina, ngakhale alimi ambiri amene adacheza ndi Uchikumbe mzigawo zonse za dziko lino adati akusimba lokoma paulimiwu pali zina zoyenera kukonza kuti phindulo libwere pambalambanda. Kadaulo pa nkhani ya ziweto kusukulu ya ukachenjede ya Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) pulofesa Timothy Gondwe komanso mkulu wa mgwirizano wa mabungwe okhudzidwa ndi ulimi la Civil Society Agriculture Network (CisaNet) a Tamani Nkhono-Mvula adaphera mphongo zonena za alimiwo. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu A Gondwe adati pakadalipano alimi a ngombe zamkaka akuchuluka koma chiwerengero cha ngombe nchochepa. +Pali zina zoyenera kusintha kuti alimi a mkaka apindule kwambiri Iye adati izi zili choncho chifukwa ambiri mwa iwo ndi angonoangono ndipo amakhala ndi ngombe imodzi kapena ziwiri. +Alimi akuluakulu sakuonetsa chidwi ndi ulimiwu. Alimi aangono ambiri alibe zipangizo komanso akusowa ulangizi pa kadyetsedwe, kasamalidwe ka ngombe komanso momwe angasamalire mkaka wawo kuti ukapeze msika wabwino, adatero Gondwe. +Adapereka chitsanzo cha ngombe ya mkaka ya mtundu wa Fresian imene itadyetsedwa bwino ikhoza kutulutsa malita 40 pa tsiku koma alimi ambiri amakama malita 10 kapena 12 okha patsiku. +Iwo adatinso vuto lina ndi ndondomeko zoyendetsera msika wa mkaka. +Pophera mphongo, Nkhono-Mvula adati imodzi mwa ndondomeko zimene zimathimba alimiwa pakhosi ndi Gawo 36 ya malamulo a bizinesi ya mkaka. +Malingana ndi lamuloli, alimi angonoangono sangagulitse mkaka wawo momasuka pokhapokha atakhala ndi njira zowiritsira yomwe ndi ntchito ina yapadera chifukwa afuna kudutsa mndondomeko zambiri kuti avomerezedwe kutero. +Pachifukwa ichi, alimiwa amakakamizidwa kukagulitsa mkaka wawo kumakampani omwe ali ndi zipangizo pamtengo wozizira, adatero iwo. +Malinga ndi mkuluyo, alimi a mkaka ali pachipsinjo cha misonkho kusiyana ndi alimi ena poti iwo amadulidwa msonkho pa ndalama zilizonse zomwe angapate pa malonda awo pomwe pamalamulo a msonkho, munthu amayenera kudulidwa msonkho ngati wapeza ndalama zoposa K50 000 pa mwezi. +Mawu a akadaulowa akungopherezera zimene alimi ena mzigawo zonse zitatu adauza Uchikumbe. +Wapampando wa gulu la Lusangazi Dairy Farmers Cooperative ku Mzimba, Hesco Banda, adati vuto la kusowa kwa zakudya likuchititsa miyoyo ya alimiwa kukhala yowawa. Iye adati ngakhale alimi ali ndi kuthekera kogula chakudya cha ngombezo pamtengo wa K10 000 thumba la makilogalamu 50, chikusowa. +Zakudya zikusowa, moti tikungogwiritsa ntchito deya. Vuto lake, deyayu tikulimbirananso ndi anzathu a ku Tanzania amene akulolera kugula deyayo pamtengo wa K500 pa kilo mmalo mwa mtengo wake wa K200, adandaula Banda. +Vuto lina, iye adati, ndi kusowa kwa msika chifukwa kumpoto kulibe kampani zogula mkaka monga momwe zilili mzigawo zina. Kampani za Lilongwe Dairy, Suncrest Creameries komanso Dairibord zimagula mkaka kumwera ndi pakati. Adaonjeza kuti izi zachititsa kuti mavenda alowererepo, pomagula mkaka pamtengo wolira. +Ngakhale msika ulipo, alimi ena, monga Thomson Jumbe wa mmudzi mwa Waruna, T/A Chimaliro ku Thyolo mitengo ndiyotsika. Malingana ndi unduna wa malimidwe, mtengo wotsikitsitsa umene mkaka uyenera kugulitsidwira ndi K155 pa lita. +Timagulitsa mkaka pa mtengo wa K150 pa lita pomwe kuti titulutse lita imodzi zimalowa ndi zambiri, makamaka tikawerengera zakudya monga deya komanso mankhwala, adatero Jumbe. +Poyankhapo pamadandaulowa, nduna ya zamalimidwe ulimi wothirira ndi chitukuko cha madzi Dr George Chaponda adati unduna wake uunika madandaulowa nkuwona kuti ungathandizane bwanji ndi alimiwa kuti ulimiwu upite patsogolo. +Padali pachiwaya cha tchipisi Adayezetsa tchipisi cha K150, ine ndidamuonjezera kuti agule cha K200. Mmenemo ndi momwe zidayambira kuti Henry Mbinga akumane ndi Chimwemwe Edwin amene tsopano amangitsa woyera. +Chiyambicho chidaoneka chachibwana, koma lero ndi nkhani ina chifukwa tsiku lililonse Chimwemwe akusisita chifuwa cha Henry mwabata, mopanda mantha kapena manyazi. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Henry yemwe akugwira ntchito ku Magic Clean adati umu mudali mu July 2014 pamene iye adapita pasukulu ya Zingwangwa Progressive mumzinda wa Blantyre. +Kumeneko iye akuti amakaonera mpira wa ntchemberembaye ndipo ako kadali koyamba kumuona Chimwemwe akusewera mpira. +Lidali Lachinayi, mawa wake ndidamuonanso pachiwaya cha tchipisi. Ndidakhotera pomwepo. Iye adayezetsa tchipisi cha K150, ine ndidauza mwini chiwayacho kuti amuyezere namwaliyo tchipisi cha K200, adatero Henry. +Komatu mtsikanayu akuti adali asakumudziwa Henry, pamenenso Henry akuti kadali kachiwiri kumuona komabe adalimba mtima kucheza naye. +Ndiyetu Henry akuti adayamba kumuperekeza uko namwaliyu akudya tchipisicho, chidakoma ndipo sichidachedwe kutha chifukwa cha tinkhani ta Henry. +Asadamalize kudya tchipisicho mawu adagwa kuti akumufuna amange naye banja, koma Chimwemwe adazinda mauwo. +Padadutsa masiku atatu pamene adagwirizana zokumananso. Zidatheka ndipo namwaliyu adavomera kuti wagwa mmanja mwa Henry. +Ndimafuna ndione ngati amanena zoona komanso ndimuone khalidwe lake, adatero namwaliyu. +Ukwati udachitika pa 27 December chaka changothachi ndipo awiriwa akukhalira limodzi mwachimwemwe. +Henry amachokera mmudzi mwa Joni, Senior Chief Somba mboma la Blantyre pomwe Chimwemwe ndi wa mmudzi mwa Chikoja kwa Senior Chief Somba komweko. +Asemphana maganizo Pa ulimi wa chamba Alimi ambiri mdziko muno ati ndi okonzeka kuyamba kulima chamba chosazunguza ubongo mmalo mwa fodya bola boma liwaunikire zomwe ayenera kuchita, koma ena akukaikirabe ngati ulimiwu ungawatulutse muchithaphwi cha umphawi momwe akusambira. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Izi zikudza pamene Nyumba ya Malamulo yavomereza bilu yopereka mphamvu kuboma kuti livomereze ulimi wa chamba chachilendochi monga njira imodzi yopititsira patsogolo chuma cha dziko lino kulowa mmalo mwa fodya. +Phungu woima payekha wa dera la kumpoto mboma la Ntchisi, Boniface Kadzamira, masiku apitawo adapempha Nyumba ya Malamulo kuti ipereke mphamvu kuboma kuti livomereze ulimi komanso kugwiritsa ntchito mtundu wina wa chamba wotchedwa industrial hemp. +Kadzamira adatsindika kuti mtundu wa chamba chomwe iye akufuna Amalawi azilima ndi ndi wosiyana kwambiri ndi mtundu wina wa chamba chozunguza ubongo chomwenso ena amapenga nacho akachisuta. +Chamba akunenacho si ngati ichi chomwe chimazunguza ubongo! Iye adati chamba chomwe akunena chakhala chikulimidwa ndi kugwiritsidwa mmaiko ambirimbiri kuyambira chaka cha 1770, ndipo maiko omwe akulima mbewuyi adatukuka kwambiri kudzera mphindu lomwe amapeza kuchokera ku malonda a mbewuyi. +Ine ndine munthu wosangalala komanso wokhutira kwambiri ndi momwe aphungu a ku Nyumba ya Malamulo adaikambirana nkhaniyi. Chamba chili ndi phindu lalikulu kwabasi. +Dziko la Malawi nalonso liyenera kuyamba kulima ndi kugwiritsa ntchito mbewuyi kuti tiyambe kupeza nawo phindu lomwe anzathu akupeza maiko enawo, adatero Kadzamira. +Ndipo pocheza ndi Msangulutso Lachiwiri, Gunde Njobvu wa mmudzi mwa Moloka mdera la mfumu Kayembe ku Dowa, adati iye ndi wokonzeka kukhala mmodzi mwa alimi oyambirira kulima mbewuyi. +Njobvu adati wakhala akulima fodya wa bale zaka zambiri, koma palibe chomwe wapindula. +Choncho, sindikuona vuto kuyesako ulimi wa chamba. Mwinanso chamba nkukhala mdalitso wanga ndipo sindikudziwa kuti ndingachite bwanji kuti ndikhale nawo mgulu la alimi oyambirira, adatero mkuluyu. +Kambiza Mwale, mlimi wa zaka 60 wochokera mdera la mfumu Kasalika mboma lomweli, adati nkhaniyi adailandira, koma ali ndi mantha kaamba koti omwe akukolezera ulimiwu nkhaniyi sadatulukire nayo poyera kuuza alimi za kusiyana kwa mbewuyi ndi chamba chosuta. +Iye adati ali ndi nkhawa poopa kudzagwa nazo mmavuto kaamba kosatsatira malamulo. +Mwale adati iye satengapo kaye gawo paulimi umenewu kufikira boma litawaunikira bwino kusiyana kwake kwa mbewu ya chamba choletsedwa ndi mbewu ya chamba chomwe chimagwiritsidwa ntchito popanga zinthu. +Towera Jere, wa mmudzi wa Mzukuzuku Jere mboma la Mzimba, naye adati sadapangebe chiganizo ngati nkofunika kuti iye atengepo gawo pa ulimi wa chamba. +Jere adati mantha ake ali poti zikamayamba, boma ndi mabungwe amagwiritsa njira ndi mawu onyengelera pofuna kukopa anthu pamene pansi pa mtima akufuna kuwagwiritsa ntchito anthu osauka podzilemeretsa. +Alimi mdziko muno agwiritsidwa ntchito ngati makasu a anamadya bwino kwa nthawi yaitali kwabasi. Pomwe ulimi wa fodya unkayamba, anthu timauzidwa kuti masomphenya athu akwaniritsidwa tikalimbikira kulima, koma ndi angati omwe akusimba lokoma lero kaamba ka phindu lochokera muulimi wa fodya? adafunsa mayiyu. +Mmodzi mwa achinyamata omwe amakhala pa Luchenza mboma la Mulanje, Violet Banda, adati iye sakuona choletsa kulima chamba chosazunguza ubongo. +K oma iye adapempha boma kuti liunikire Amalawi ngati kagulitsidwe ka mbewuyi kadzasiyane ndi momwe zilili ndi fodya wa bale ndi mitundu ina. +Ndikunena ichi kaamba koti ndikutha kuona alimi atapatsidwanso chiyembekezo chabodza kuti miyoyo yawo idzasintha kudzera muulimi wa chamba. Ayenera kutiuza kuti kodi adzagule chamba ndani, ndipo akusiyana bwanji ndi omwe akugula bale kuokushoni lero? adatero mtsikanayu. +Mkulu wa bungwe la Community Initiative for People Empowerment (Cipe) Trintas Manda adati alibe chiyembekezo kuti dziko la Malawi lidzatukuka kaamba kolima chamba. +Manda, yemwe bungwe lake limagwira ntchito zake ku Mzimba ndi Kasungu, adatsindika kuti pokhapokha boma la Malawi litathetsa chiyengo chomwe chikuchitika pamsika wa fodya, dziko lino lidzapitirirabe kulirira kuutsi zokolola zili zake. +Woyendetsa ntchito za bungwe la National Initiative for Civic Education (Nice) mboma la Nsanje Kondwani Malunga adati iye akugwirizana ndi zoti pakhale ndondomeko yapadera yodziwitsira anthu za kusiyana kwa chamba choletsedwa ndi chomwe dziko lino likufuna lichivomereze. +Anthu ayenera kuphunzitsidwa mokwanira kuti azitha kusiyanitsa pakati pa chamba choletsedwa ndi chomwe boma likufuna kuchivomereza. Apo ayi, tidzaona mavuto ambiri kuposa phindu lomwe dziko lino likuyembekezera kupeza kudzera muulimi umenewu, adatero Malunga. +Aphungu angapo ati akugwirizana ndi ganizo loyambitsa ulimi wa chamba mdziko muno. +Koma ena, monga Lucius Banda, yemwe ndi phungu wa dera la kumpoto mboma la Balaka, wati monga munthu sangasiyanitse mowa wamasese ndi thobwa, padzakhala povuta kuti anthu asiyanitse mtundu wa chamba chosuta ndi chogwiritsa ntchito kupanga zinthu. +Choncho, pamene tivomereza biluyi, nkofunikira kuti tiikenso ndondomeko zapadera zomwe zingatsogolere mabwalo a milandu pozenga mlandu omwe angafune kupezerapo mwayi lamuloli, adatero Banda. +Ndipo mkulu wa bungwe la Drug Fight Malawi (DFM) Nelson Baziwelo Zakeyo wati sakugwirizana ndi zomwe achita aphungu a Nyumba ya Malamulo povomereza biluyi, ponena kuti izi zidzabweretsa chisokonezo mdziko muno. +Anatchezera: Akukana kunditsata Agogo, Ndine mnyamata wa zaka 20 ndipo ndili pachibwenzi ndi mtsikana wa zaka 22 ndipo timakondana kwambiri koma vuto ndi loti akukana kunditsata kuchipembedzo changa. Ndiye ndithetse chibwenzichi kapena ndipitirize? Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu RM Zikomo RM, Choyamba ndikanakonda nditadziwa kuti cholinga cha chibwenzi chanu ndi chiyani, komabe poti ukufuna maganizo anga ndikuuza. Ndikhulupirira kuti cholinga cha chibwenzi chanu ndi kudzamanga banja mtsogolo, ngati sindikulakwa, ndipo ngati anthu muli ndi cholinga chodzakhala thupi limodzi ndi bwino kwambiri kuti muzigwirizana muzonse. Inde, pali mabanja ena oti mwamuma amapemphera mpingo wina ndipo mkazi nayenso amapita kwina, nkumakhala bwinobwino mwansangala. Koma kunena zoona mukasiyana zipembedzo pamakhalabe kenakake kosonyeza kuti pali kusagwirizana mbanjamo. Ndiye ndi bwino kugwirizana chimodzi musanalowe mbanja. Munayamba mwakhala pansi nkukambirana kuti chifukwa chake nchiyani akukanira kukutsatira kuchipembedzo chako? Nanga iweyo sungamugonjere wachikondi wakoyo kuti umutsate kumpingo kwake? Nchifukwa chake nthawi zambiri kumakhala bwino inu achinyamata mukamafuna mnzanu wachikondi muzidyerera maso kwa anyamata kapena atsikana omwe mumapemphera nawo mumpingo umodzi. Nanga chokafunira wachikondi kwina nchiyani? Ndiye wafunsa kuti kodi uthetse chibwenzichi kapena ayi? Ine ndikuti zili ndi iwe mwini mmene ukumvera mumtima mwako. +Ndipange bwanji? Agogo, Ndine mnyamata wa zaka 20 ndipo ndinakwatira mwangozi nditapereka mimba kwa mtsikana wina. Ndimafuna nditapitiriza sukulu koma zikukanika chifukwa mkaziyu akukana kuti nditero. Ndipange bwanji? JK Zikomo JK, Ndakhala ndikulangiza anyamata ndi atsikana ambiri kuti mfulumiza adadya gaga, lero si izi waziona, mwana wanga? Ndakondwa kuti waona wekha kufunika kwa sukulu ndi kuipa koyamba kugonana ndi atsikana, komanso mosadziteteza, udakali pasukulu. Udakali msinkhu wopita kusukulu ndipo ndi bwino kwambiri utatero. Ngati mkazi wakoyo umamukonda ndipo iyenso amakukonda chimodzimodzi, ayenera kumvetsa cholinga chako choti upitirize maphunziro ako kuti kutsogolo mudzakhale moyo wabwino, wodzidalira nokha, osati mmene zilili panopa chifukwa mmene ndikuonera banja lanu lidalira makolo-chakudya, zovala, sopo amene ndi zina zotere. Umutsimikizire mkaziyo kuti kupitiriza sukulu sikutanthauza kuti banja lanu latha, koma kuti ukuganiza za tsogolo lanu ngati banja. Umuuze kuti sukulu simatha-akuluakulu amene mukuwaona mmaofesiwa ambiri afika pamene ali chifukwa chopitiriza sukulu ali mbanjabe. Tsono chovuta kuti iwe upitirize sukulu nchiyani? Ngati iye safuna sukulu, zake izo, iwe chita zomwe ukufuna. Ndikhulupirira ngakhale makolo ako adzasangalala kwambiri kumva kuti ukufuna kupitiriza sukulu. +Ndinalapa Anatchereza, Ndinali mchikondi kwambiri ndi mwamuna wa kwa Jali koma atandipatsa pathupi samandiuza nzeru iliyonse yothandiza pa umoyo wa mwana wodzabadwayo, mapeto ake anandipatsa ndalama zokachotsera pathupipo kuchipatala. Zotsatira zake ndinadwala kwambiri koma nditapeza bwino anayamba kundipepesa koma ine ndinamenyetsa nkhwanga pamwala kuti sindidzayambiranso. Kodi mwamuna wotsogolera zolakwa ndi wabwino? Koma ineyo ndinalapa, amama, ndipo ndinasiyana naye. +ML Zikomo ML, Ine ambiri ndilibe koma ndingoti khokhokho! Kumeneko ndiye timati kukula. Akulu akale adati mmphechepeche mwa njovu sadutsamo kawiri. Munthu ukachimwa ndi bwino kulapa monga wachitira iweyomu. Ndithudi mwamunayo sadakufunire zabwino ndipo chikondi chake chidali cha chiphamaso, basi; amangofuna zogonana koma osalabadira za zotsatira zake. Wachita bwino kumusiya ameneyo ndipo yamba moyo wina watsopano. Mwamuna wina akakufunsira mulole, koma osamulola kuti muyambe mwagonana musanalowe mbanja. Amuna ambiri akangowavulira musanalowe mbanja, sakhalanso ndi chidwi chifukwa amati ngati wandilola, nkutheka kuti adalolanso amuna ena. +Dovu lakula ku nsanje Anthu ena mboma la Nsanje alephera kupirira nkhuli ndipo akuphabe ndi kugulitsa nyama ya ngombe, mbuzi, nkhumba ndi nkhosa mozemba motsutsana ndi chiletso chomwe unduna wa zamalimidwe udakhazikitsa pofuna kuthana ndi matenda a zilonda za mmapazi ndi mkamwa (foot and mouth disease) omwe adabuka mbomalo miyezi itatu yapitayo. +Escom in free-for-all fuel scam Wait gets longer Secrecy over party funders Unduna wa zamalimidwe udaletsa kupha kapena kugulitsa ziwetozi mbomali pa 8 January malinga ndi kubuka kwa matendawo, koma ngakhale chiletsochi sichidachotsedwe, anthu ena akuphabe ngombe ndi ziweto zina ndi kugulitsa nyama mozemba, zomwe zikupereka chiopsezo kuti matendawo atha kukhodzokera maboma ena. +Senior Chief Malemia wa mbomali watsimikiza kuti izi zikuchitikadi ndipo wauza achitetezo mmidzi kuti agwire aliyense amene amupeze akuchita izi. +Malire a Nsanje ndi Chikwawa amayenera kuponda mankhwala Vuto lake anthuwa akumapha ziweto mozemba, ndiye zikuvuta kuti tiwagwira bwanji, komabe tikuwafufuza ndipo tikawapeza tiwagwira, adatero Malemia. +Pocheza ndi Msangulutso palamya posachedwapa, Ernest Msambo wa ku Fatima kwa T/A Mlolo mbomalo adavomereza kuti kumeneko anthu akupha ziweto ndi kugulitsa nyama yake motsutsana ndi chiletso cha boma. +Achimwene, lija nkale adaletsa kuti anthu azipha ndi kugulitsa nyama, nkhuli yavuta, komanso anthu a kuno timadalira kupha kapena kugulitsa ziweto kuti tipeze ndalama, nchifukwa chake anthu akuchita izi mwakabisira. Pamsika nyama sungaipeze, koma mupeza mmakomo anthu akudya nyama, adatero Msambo. +Koma yemwe akulondoloza momwe nthendayi ikuyendera, Dr. Patrick Chikungwa, adati uku nkulakwa ndipo ngati anthuwa samvera lamulo la boma matendawa atha kufalikira dziko lonse. +Panopa tili mkati mothana ndi matendawa, ndiye ngati ena akuchita zithu mosemphama ndi ndondomeko yomwe takhazikitsa, asokoneza zomwe tikuchita. Adziwe kuti matendawa angathe kufalikira dziko lonse ngati anthu akuzembetsa ziweto kapena nyama pogwiritsa njira zamadulira, adatero Chikungwa. +Maboma ena monga Blantyre, Zomba, Mwanza, Mulanje ndi Thyolo kuchigawo cha kummwera amadalira nyama yochokera mboma la Nsanje ndi Chikwawa. +Malire a bomali ndi Chikwawa pa Sorjin komanso pa Phokera ndi Mtayamoyo paikidwa zipata za mankhwala a madzi omwe munthu aliyense ngakhale galimoto ikamatuluka mboma la Nsanje, akumapondapo kuti asalowetse matenda mmadera ena. +Koma Chikungwa wati izi sizingathandize kwenikweni ngati ena akudzerabe njira zina osadzera pazipatazi. +Apapa ndiye kuti angathe kulowetsa nyama mmaboma ena podutsa njira zachidule. Ikalowa mmadera ena ndiye kuti nakonso kufika matendawa ndiye kuthana nawo kwake kudzakhala kovuta kwambiri, adatero Chikungwa. +Iye adati kufika lero, achita katemera katatu mbomalo ndipo akudikira kuti aonetsetse ngati nthendayi yatheratu asadalengeze kuti anthu ayambe kupha ndi kugulitsa ziweto zawo. +Matendawa amapha ngombe koma nanga nchifukwa chiyani aletsanso kuti nkhosa, nkhumba ndi mbuzi zisamaphedwe? Nzoonadi, kuti matendawa amagwira maka ngombe, koma ziweto zinazi zili ndi kuthekera kofalitsa matendawa. Mwachitsanzo, nkhumba ndi imene ili pachiopsezo chachikulu kufalitsa matendawa. +Pofuna kuti matendawa tiwamalize mosavuta, tidaletsadi kuti ziweto zinazi zisatuluke mbomalo komanso zisaphedwe ncholinga choti pasakhale kufalikira kwa matendawa, adatero Chikungwa. +Iye adati ngombe ikagwidwa ndi matendawa, imatenga sabata ziwiri kuti iyambe kuonetsa zizindikiro zoti ikudwala. Ikagwidwa ndi zilonda za mmapazi komanso kukamwa imalephera kuyenda ndi kudya ndipo zikatero imafa. +Malinga ndi ofesi ya ziweto muunduna wa zamalimidwe, boma la Nsanje lili ndi ngombe 40 000, mbuzi 147 000, nkhosa 3 000 ndi nkhumba zoposa 20 000. +Boma la Chikwawa nalo lidakhudzidwa ndi matendawa ndipo ngombe 91 965 ndizo zidalandira katemera mchigawo choyamba cha katemerayo. +Adakumana bwanji mchakacho? Ankadzapepesa maliro a mkazi wanga Ukwati ndi chinthu chabwino, ndipo Mulungu amasangalala nacho. Chaka cha 2015 Mulungu adadalitsa ena ndi mabanja ndipo lero tingochita molawitsa mwa ochepa amene adalandira madalitso olowa mbanja. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Precious ndi Kachingoni kake patsiku la chinkhoswe Tiyambe ndi Excello Zidana amene adakumana ndi nthiti yake Katerina Mtambo kudzeranso mmphamvu ya Mulungu. +Zidana, mkonzi wa pologalamu ya Ulimi Walero ku MBC, adakumana ndi nthiti yakeyi malo angapo koma nthawi yeniyeni idali pamene Katerina amakapepesa Excello pa imfa ya mkazi wake. +Katerina adataya wokondedwa wake chimodzimodzinso Excello. Awiriwa akuti adapepesana za imfayo koma kumapeto kwake adatolana ndi kumangitsa woyera. +Kudali kosoketsa nsapato Wina waluso pakapezedwe ka namwali ndi Richard Chipuwa, goloboyi wa Be Forward Wanderers. +Kuonongeka kwa nsapato ya Chipuwa udali mwayi, poti pokakonzetsa nsapatoyo adakabatha namwali yemwe adapangitsa naye chinkhoswe mchaka changothachi. +Kukumanako akuti kudali kosavuta koma kuti asoke Chichewa chokhetsa dovu la Dinnah Hxaviel ndiye idali ntchito yoposa kukhala pagolo. +Ngakhale mayi a njoleyi amaletsetsa mwana wawo kuti asayerekeze kuyenda ndi anyamata, koma nthawi idakwana kutinso makolowo sakadakwanitsa kuletsa pamene adakumana ndi mwamuna weniweniyu. +Adali kasitomala wanga wa tchipisi Wina ndi Steve Nthala yemwe ndi mkulu wa nyimbo mgulu la Area 36 Anglican Choir ku Lilongwe amene adapeza njole yomwe idali kasitomala wake wa tchipisi. +Iye akuti adagwa mchikondi ndi Chrissy Malipa yemwe adali kabwerebwere wa tchipisi chomwe mnyamatayu ankakazinga pachiwaya. +Steve akuti namwaliyu amati akamadzagula tchipisi pachiwaya chake mtima umagunda ndipo amangomuyezera chambiri. Chidali chiyambi mgwirizano wolowa mbanja. +Timakayangana osewera mpira ku Kasungu Ulendo wa timu ya Surestream wokayangana osewera mboma la Kasungu udali waphindu kwa Team Manager wa timuyi Honest Nkhwazi. +Honest adapeza chamwayi kuti asodzekonso Chisomo Nkhoma, yemwe ndi wapolisi papolisi ya Kasungu kuti akhale wachikondi wake. Sadaope yunifomu ya polisi, pali chikondi palibe mantha. +Awiriwa adachititsa chinkhoswe mboma la Kasungu ndipo amangoyembekezera kuti ukwati tsopano uchitike, abusa agwire ntchito yodalitsa awiriwa. +Awa ndi ochepa chabe amene tidawatulutsa patsamba lino kutifotokozera omwe adakumanirana ndi okondeka awo. Mchakachi achite mphumi ndani? Dzina la Yesu ndilo lidachititsa Akulu adati dzina limapereka kapena kulanda mwayi wa munthu ndipo izi nzoonadi, taonera pa Noel Nthala, yemwe mumzinda wa Lilongwe amadziwika ndi dzina lakuti Yesu ndipo ndi mmodzi mwa masapota akuluakulu a timu ya Silver Strikers. +Anthu ambiri mumzinda wa Lilongwe amakhala ndi chidwi akamva za Yesu poganiza kuti mwina ndiye wa ku Yerusalemu ndipo ichi ndicho chidatchukitsa mnyamatayu yemwe pano wapeza nthiti Zuziwe Nyondo. +Kukumana kwa Nthala ndi Zuziwe mwina sikungadabwitse chifukwa monga anthu ambiri mumzindawu amazizwa ndi dzinali nkutheka namwaliyu naye amafunitsitsa atamuona. +Ndimamuona ndikamachokera kuntchito koma tsiku lina nditalimba mtima ndidamuimitsa nkumulonjera. Nditamuuza dzina langa adaoneka wodzidzimuka koma ine sindidatengere zimenezo, mtima wanga udali pa iyeyo basi, adatero Nthala. +Naye Zuziwe adati dzina lokhalo amangolimva koma samadziwa kuti munthu wake nkukhala mmene amawonekera Nthala, ayi. +Amatsutsanabe zamakumanidwe awo Ambiri akapezana nkukondana nkugwirizana za banja amakhala ndi chikumbumtima cha komwe ndi mmene adakumanirana, koma ndi nkhani yochititsa chidwi kumva za Chiyembekezo Focus Maganga ndi Lydia Kalonde. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Awiriwa akuti mpaka lero sagwirizanabe za malo ndi tsiku lomwe adakumana koyamba ndipo chomwe amakumbukirako nchakuti mudali mchaka cha 2013 ndipo adapanga chinkhoswe pa 7 June 2013. +Chomwe ndimakumbuka ine nchakuti ndidakamupeza kuofesi yake nditapita ndi mnzanga Dickson Kashoti pomwe iye amakakamira kuti tidakumana koyamba mminibasi koma kwa ine uku kudali kukumana kwachiwiri, adatero Focus. +Focus ndi Linda pachinkhoswe chawo Panthawiyo nkuti Focus akugwira ntchito ya utolankhani pomwe Lydia adali wothandizira mkulu wa zofalitsa mawu kuunduna wa zofalitsa mawu komwe ali mpaka pano. +Focus adati poti awiriwa alibe tsiku lokhazikika lomwe angati adakumana koyamba, chomwe amakumbukira nchakuti atakumana kuofesi ya Lydia adangopatsana moni polingalira kuti idali nthawi ya ntchito. +Kwinaku akuti amakumbukira kuti atakumana mminibasi Lydia adali ndi chidwi ndi momwe iye adavalira, suti yapamwamba koma tsitsi losapesa ndipo mmaganizo mwake amangoti mwina wadzuka ndi mowa mmutu. +Ngakhale adali ndi maganizo oterewa, macheza adayenda bwino mpaka posiyana tidapatsana nambala za foni nkumaimbirana mwakathithi mpaka chibwenzi chidayamba, adatero Focus. +Iye adati chitachitika chinkhoswe iwo adalowana asadapange ukwati pofuna kukonzekera mofatsa ndipo akuti ukwatiwo ukhalako kumapeto kwa chaka chino. +Focus akuti amakonda kwambiri Lydia chifukwa ndi wooneka bwino, wanzeru, wachikondi, woopa Mulungu komanso amamuthandiza nzeru ndi kumulimbikitsa akamafooka. +Naye Lydia akuti amamukonda kwambiri Focus kaamba ka zochitika zake komanso masomphenya ndi kulimbikira pochita zinthu. +Amapanga zondisangalatsa komanso ali ndi khama ndi luntha pochita zinthu. Tidapezana okonda kupemphera tokhatokha komanso ansangala, adatero Lydia. +Dyson Gonthi: Msangalatsi wa pakanthawi Kwa amene tidabadwa pakanthawi Dyson Gonthi ndilo dzina limayambirira kubwera mumtima tikamva tingoma ndi kanyimbo ka Nzeru Nkupangwa komanso ambiri tamumvapo akuwerenga ndi kuulutsa mawu pawayilesi ya boma ya Malawi Broadcasting Corporation (MBC-Radio 1). Zambiri za mkuluyu zidakhala ngati zidakwiririka kaamba ka kukula nkupuma pazochitika. +STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere: Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Gonthi: Zisudzo ndidayamba kalekale Tikudziweni bwana. Dzina langa ndi Dyson Gilbert Gonthi, ndimachokera mmudzi mwa Kasiya kwa Mfumu yaikulu Chilooko mboma la Ntchisi. Kunena za maphunziro aaah, sindidapite patali ndidalekezera Fomu 4 pa Robert Blake ku Dowa mchaka cha 1966. +Nanga mbiri yanu ya ntchito ndi yotani? Ntchito ndidayamba mc h a ka cha 1966 nditangomaliza sukulu. Ntchito yanga yoyamba idali yogula mbewu kumsika wa Admarc ku Nasawa. Nditagwirako pangono, ndidaganiza zokapitiriza maphunziro ndiye ndidauyamba ulendo wa ku Uganda koma ndidabwererera ku Norton mdziko la Zimbabwe chifukwa cha zovuta zina makamaka zikalata zoyendera. Nditabwerera, ndidalowa mboma kunthambi ya zofalitsa nkhani ya Malawi News Agency (MANA) mchaka cha 1967. Ndidagwira kumeneku mpaka mchaka cha 1970 pomwe ndidapita ku MBC mpaka kupuma koyamba. +Mukutanthauzanji mukati kupuma koyamba? Ndikutero chifukwa mc h a ka cha 1993 ndidabwereranso ku MBC komweko komwe ndidagwira mpaka mchaka cha 2006 pomweno ndidapumiratu chifukwa cha kukula. +A n t h u a k h a l a n s o akukumvani mukuchita zisudzo, mungatiuzepo zotani pamenepa? Nzoonadi ndimapanga zisudzo ndipo ndidayamba kalekale ndili wamngono. Ndikakhala pakati pa anzanga ndimakhala msangalatsi wawo ndiye ndidaona kuti ndingopitiriza kuchita zisudzo. Pachifukwa ichi ndidayambitsa gulu langa la zisudzo la DYGO Drama Group potengera dzina langa la Dyson Gonthi, komaso ndachitapo z isudzo ndi magulu osiyanasiyana pawayilesi ndi mmalo ena. +Anatchezera Amandikakamirabe Agogo, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndine mtsikana wa zaka 19 zakubadwa, vuto langa ndi lakuti pali mnyamata wina wake amene amandifuna koma ineyo sindimamufuna olo pangono. Iye samafuna kuti angondisiya moti pano miyezi iatatu yakwana akundifunabe. Nthawi zina ndimayesetsa kuti ndimuonetse nkhope yosangalala koma mtima wanga umakana. Ndiye nditani poti ine ndili naye kale amene ndimamukonda ndi mtima wanga wonse? Chonde ndithandizeni. +Zikomo mtsikana, Ndikuthokoze kwambiri chifukwa cha maganizo ako abwino. Ndithudi akadakhalapo atsikana ambiri amaganizo ngati akowa bwenzi zinthu zikoma. Atsikana ambiri masiku ano amakonda kukhala ndi zibwenzi zambirimbiri ati kuti pamapeto adzasankhepo mmodzi. Chimenecho si chikondi ndipo mapeto ake ambiri amasokonezeka, mwinanso kutenga pathupi pa mnyamata amene samamukonda. Apa iwe waonetsa kale kuti ndiwe wokhwima mmaganizo ndipo ndikufuna kuti ndikulimbikitse kuti chikondi sakakamiza. Ngati uli kale ndi mnyamata amene umamukonda ndi mtima wako wonse palinso chifukwa chanji choti uzitaya nthawi ndi wina amene ulibe naye chidwi? Komabe nthawi zina chimachitika nchoti amene umamukonda kwambiri iye alibe chikondi, angofuna kukuseweretsa ndi kukometsa mawu a pakamwa ndipo amene sukumukonda ndi amene ali ndi chikondi chozama pa iwe. Ndiye apa chimene ungachite uyambe waona kuti bwenzi lakolo ndi munthu wotani? Ndi wamakhalaidwe otani? Ndi waulemu kapena ayi; ndi yo kapena wodzilemekeza; cholinga chanu ndi chiyani pa ubwenzi wanu? Chimodzimodzi amene ukuti akukukakamira chibwenziyo, kodi ndi munthu wotani? Cholinga chake ndi chiyani? Ndi wakhalidwe kapena mvundulamadzi chabe? Ukalingalira zonsezo bwinobwino mpamene ungasankhe chochita, chifukwatu nthawi zina umatha kukakamira mtunda wopanda madzi nkusiya munthu wachikondi weniweni. +Gogo wanga, Ndithandizeni. Ine ndinapeza bwenzi chaka cha 2010 ndipo adapita ku Joni chaka chomwecho. Foni amaimba, inenso ndimaimba koma amangoti ndibwera pompanopompano koma kuli zii! Amandiuza zolimbitsa mtima ndipo ndili pano ndakana amuna ambiri mpakana ena kufika pomandinena kuti ndine chikwangwani. Agogo, ndizidikirabe? AK, Lilongwe. +Kudali ku Presbyterian Church of Malawi Kudali kuphwanya mafupa ku Dream Centre Assemblies of God mumzinda wa Blantyre Loweruka pa 2 May pamene Faith Mussa amachititsa ukwati ndi bwenzi lake Brenda Chitika. +Ndi kanamwali kopanda banga, kopanda chipsera. Thupi losalala komanso kathupi lomva mafuta. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ikokatu ndi ka mmudzi mwa Sikoya kwa T/A Chikumbu mboma la Mulanje. Iko ndi kachinayi kubadwa mbanja la ana asanu. +Faith Mussa kuimbira namwali wake kanyimbo kachikondi Faith amene adatchuka kwambiri ndi nyimbo ya Desperate, akuti ubongo wake udasokonekera pamene adaona njoleyi Lamulungu mu 2009 pomwe mnyamatayu adapita kumpingo wa Brenda wa Presbyterian Church of Malawi (PCM) mumzinda wa Blantyre kukatsitsimuka. +Faith adatsitsimuka zenizeni chifukwa kusalalanso kwa njoleyi kudaziziritsa mtima wake. Tsikuli Mulungu adakumana ndi chosowa chakedi. +Ndili mumpingomo foni idaitana ndiye ndidapita panja kukayankha. Ndili panjapo kulankhula pa fonipo, ndidaona namwaliyu chapakataliko akutonthoza mwana, akutero Faith. +Maso adali pa namwali, khuku lidali pa foni. Iye samasunthika ndipo pena Brenda akuti amathawitsa diso lake kuti asaphane maso ndi mnyamatayu koma Faith samasunthika. +Izi zidatanthauza kanthu kena mumtima mwa Faith ndipo nkhani yonse idakambidwa patangotha mwezi. +Titaweruka, ine ndi mchimwene wanga tidaperekeza namwaliyu. Ndinene apa kuti mwana amatonthozayo sadali wake. +Poyamba Brenda amacheza ndi mbale wanga ndiye pamenepa ndidadziwiratu kuti ndikuyenera kuchita kanthu, adatero Faith. +Pangonopangono awiriwa adakhazikitsa macheza ndipo Faith sadachedwetse koma kugwetsera mawu oti adzalumikize awiriwa kukhala banja. +Padatha nthawi kuli zii, za yankho tidakayika koma pa 28 August 2009 ndidangolandira foni kundiuza kuti wagwirizana ndi [mbalume] zomwe ndidamuuza, adatero Faith wachiwiri kubadwa mbanja la anyamata atatu. +Tinkapita kumpira wa Silver Ena akangomva za masewero ampira amalingalira zogenda, kuvala ziyangoyango kapena kuimba nyimbo basi komatu monga zochitika zina zilizonse, iyi ndi nthawi yokumana ndi anthu osiyanasiyana okonda zinthu ndi zochita zosiyanasiyananso. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Onse amakonda timu ya Silver: Daniel Kudzera mumtendere woterewu, ena amachita mwayi waukulu pamoyo wawo mwina mpaka kupeza nthiti yawo monga momwe zidakhalira ndi Daniel Nthala wa mmudzi mwa Yesaya, kwa mfumu yaikulu Kalumbu ku Kamphata mboma la Lilongwe ndi Mary Kaliati. +Awiriwa akuti adakumana ali pasukulu ya Nkhoma pomwe onse ankaphunzira ndipo apa adali paulendo wopita kukaonerera masewero a timu ya Silver Strikers ndipo mwamwayi zidachitika kuti onse ankasapota timu yomweyo. +Ine ndinkapita kukaonerera mpira ndiye patsogolo panga ndidaona munthu akulowera njira yomweyo. Pokhala munthu woti ndinkamuona pasukulu, ndidamuthamangira ndipo nditamufunsa komwe ankapita adandiyankha kuti adali paulendo wa kumpira, adatero Daniel. +Iye adati apo awiriwo adayendera limodzi ndipo ali mnjira atazindikira kuti onse amakonda timu imodzi ubale udayambika pomwepo moti ankatengana nthawi zonse kukakhala mpira kukaonerera limodzi. +Nditaona chidwi chake pampira komanso nditakhutira kuti zokonda zake ndi zanga ndi zofanana ndidaona chanzeru kuti tidzasungane ndipo nditamuuza, adagwirizana ndi maganizo anga,adatero Daniel. +Mary adati iye ataona zomwe Daniel amakonda sadachotsere kuti adakumana ndi munthu yemwe angadzasungane naye popanda mavuto ndipo mwamaganizo akewo zidayendadi choncho mpaka pano akukhala limodzi ngati banja mokondwa. +Zidangokhala ngati kuti ndife mapasa chifukwa zambiri zomwe ndimakonda, nayenso amakonda zomwezo monga kuleza ntima, khama pa zinthu ndi kukonda masewero ampira komanso timu yathu kukhala imodzi ndi chinthu chondisangalatsa kwambiri, adatero Mary. +Awiriwa adamaliza zilinganizo zonse zoti anthu nkutengana ngati bambo ndi mayi ndipo pano ndi banja la ana atatu ndipo akuti anawonso akuyenda mmapazi mwa makolo kukonda timu ya Silver Strikers. +Chikondi chomwe awiriwa ali nacho pa timu yomwe amasapotayi nchodabwitsa chifukwa akuti timuyi ikapanda kuchita bwino ngakhale chakudya onse awiri sachifuna mpaka kumatheka kugona nayo chakudya akuchiona. +Ulimi wamthirira usangokhala nyimbo Mkonzi, Ndimamva chisoni njala ikamagwa mdziko muno chifukwa choti mwagwa chilala pamene tili ndi nyanja ndi mitsinje yambiri yomwe simaphwera nthawi yachilimwe, zomwe zingatithandize paulimi wamthirira. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mthirira ungatipulumutse Kodi, Amalawi anzanga, ndi zoona tizifa ndi ludzu mwendo uli mmadzi? Ndithudi maiko a anzathu amene sadadalitsidwe ndi nyanja ndi mitsinje ngati ku Malawi kuno amaseka chikhakhali akationa tikupempha chakudya kumaiko ena chonsecho tili ndi kuthekera kopeza chakudya chokwanira chaka ndi chaka choti chikhoza kudyetsa fuko la Malawi chaka chathunthu popanda vuto lililonse. +Vuto ndi boma lathu lomwe limatsogoza ndale kuposa chitukuko cha dziko ndi miyoyo ya anthu ake. Ndi liti lija adayamba za kulimbikitsa ulimi wamthirira pofuna kuthetsa vuto la njala mdziko muno? Tonse tikudziwa bwino za nkhambakamwa ya Green Belt Initiative. Ndani lero angandilozere kuti Green Belt ili apa? Tidamva zoti boma lagula mathirakitala kuchokera ku India kuti athe kuthandiza alimi mmidzimu pachitukuko cha ulimi. Ali kuti ndipo akuchita nawo chiyani pano? Kugula chakudya kumaiko akunja pofuna kudyetsa fuko la Malawi kuli apo, ndi bwino koposa kuti boma likhazikitse mfundo zolimbikitsa ulimi wamthirira mmbali mwa nyanja ya Malawi ndi kuchigwa cha Shire komanso mmbali mwa mitsinje ina monga North ndi South Rukuru, Runyina, Limphasa kuchigawo cha kumpoto; mitsinje ya Linthipe, Lilongwe ndi Bua mchigawo cha pakati; mitsinje ya Thutchira ndi Ruo kummwera mongotchurapo malo ochepa. +Leo Mpulula: Alibe 2 koloko Akulu, ligi ikuyamba, inu ngati kochi wa Max Bullets mwakonzeka bwanji? Tapimana ndi matimu ambiri, zikuonetsa kuti anyamata agwira ntchito momwe ndikufunira. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mudasewera ndi Wanderers, masewero adali bwanji? Adali bwino, anyamata akuonetsa kulimba mtima, kusonyeza kuti ntchito igwirika. +Masewero atatha, mudawayankha atolankhani zamwano, vuto lidali chiyani? Mpulula: Ndazitaya Amwene, si mwano, koma atolankhani ena amadabwitsa. Adandifunsa kuti anyamata anga sadamenyere pagolo chifukwa chiyani. Ndiye ndidamufunsa kuti Wanderers idamenyera pagolo? Yekha adaona, ndiye amafuna chiyani? Amafuna timu ithe kapena? Nanga bwanji apapa mwandiyankha momwe masewero adathera? Inu kudalibe, komanso mtima wanga wakhala pansi ndipo ndapeza chomwe chidavuta, koma mudakandifunsa komweko ndiye mudakaona kuti ndi mwano koma chili chilungamo. +Mukafunsidwa momwe masewero mwawaonera, nthawi zonse mumabweza funso, pali vuto kodi? Akandifunse momwe ndawaonera? Iyeyo adali kuti? Ndipo ngati iyeyo adaonera, bwanji osakalemba zomwe waonazo? Ndimabweza chifukwa si funso ayi. Nchimodzimodzi kumafunsa kuti madziwa akupezeka bwanji kubafaku. Ine ndiye ndiziti chiyani? Akudziwa kuti timu sili bwino, ndiye akufunsa kuti ndaiona bwanji? Iyeyo adali kuti? Akufuna chiyani? Yankho ali nalo koma akufunsanso, ndiye akufuna chiyani, amwene? Amwene, koma ndamva kuti mwazitaya ku Max Bullets, zoona? Kwambiri kwake. Ndazisiya. Amwene, mwini wake wa Max Bullets, Max Kapanda, samva za munthu ndiye ndangoti khala nayo timu yakoyo, ndapita. +Nkhani yake? Ndinamuuza kuti apereke ma contract abwino kwa ma players koma iye amati player aliyense asayinire K100 000 kwa zaka zitatu, zoona zimenezo? K100 000 ndi chiyani kwa player wa mu Super League, si salale ya pamwezi imeneyo? Ndiye ma players amene ndimafuna anakana kusayinira K100 000 ndipo anapita ndiye inenso ngati kochi ndinangoti ngati ma players apita ndiye nditsala ndi nda? Nchifukwa chane nane ndachoka ku Max Bullets. Ubwino wake sindinasayine contract. +Akwawo ankati Ichocho ndi choopsa Ntchito ndi maonekedwe a Yasin Ichocho Suwedi, mmodzi mwa akatswiri pankhani yofufumitsa minyewa, ndizo zidali zolepheretsa kuti akwatire Fatima Assed Chipoka, namwali amene maso ake adamulozera. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ichocho, amadziwika kwambiri ndi kunyamula zitsulo komanso kufufumitsa minyewa zomwe akwawo kwa Fatima samakondwera nazo kuti mwana wawo atengane ndi mwamuna wotere. +Koma danja la Mulungu likalemba lalemba, njira idapezeka kuti zomwe zidalembedwazo zikwaniritsidwe pamene awiriwa adakwatirana. +Banja la Ichocho lili ndi ana atatu tsopano Kodi mkuluyu adakumana ndi zokhoma zotani? Ntchito idayamba mu 2008 pamene iye adali ndi lingaliro lokhala pabanja. Monga Msilamu, mkuluyu ankafunanso kachisilamu. +Mu April akuti adakumana ndi Fatima. Atangomuthira diso, thupi lake ngakhale lili la dzitho komabe lidazizira, nthumanzi idamenya nganga yake, akuti adadziwa kuti waona mngelo wake. Umo mudali mumsika wa Ndirande. +Kodi ndi Msilamu? Nanga bwanji sadavale hijabu? adadzifunsa Ichocho. Ndidamufunsa dzina ndipo lidali la Chisilamu, aaaa! Thupi lidalefuka, nkhani zachikondi zidalenga ngati msozi mthupi mwake. Nkhondo ya mawu idayambika. +Chifukwa cha maonekedwe ake ali oopsa, mbalume zonse zidaomba khoma chifukwa akwawo kwa Fatima adakana. +Ngati ufuna chikakuphe chita zomwe ufunazo, adatero Fatima kutsanzira momwe akwawo adanenera. +Tiatsikana tinanso tidamuuza Fatima kuti asalole. Koma chikondi chilibe maonekedwe, tsiku lidakwana kuti zolembedwa zikwaniritsidwe. Ntchito yawo yonyamula zitsuloyi ndi yomwe aliyense amadana nayo. +Kumapeto kwa 2009 adafewa mkamwa. Anthu amati ndi wandewu koma sindimaona zimenezo, ndidalola ngakhale ena amandiletsabe. Pali chikondi palibe mantha, adatero Fatima July 2010, chinkhoswe chidatheka. Lero mnyumbamo mwatuluka mphatso zitatu ndipo Fatima watsimikiza kuti Ichocho si munthu wandewu. Zomwe amaopa anthu zija sizichitikamo mbanja lawo. +Koma mu 2013 nkhondo mnyumbamu idabadwa. Mkaziyu akuti amakanitsitsa kuti asamakachite nawo mpikisano wofufumitsa minyewa (body-building) chifukwa akamachita mpikisanowu amavala timakabudula tamkati tokha, zomwe sizigwirizana ndi Chisilamu. +Ndidayesera kumupatsa zitsanzo kuti si tchimo ndipo pano zonse zili tayale, adatero Ichocho, yemwe akuti amene amachita masewero ofufumitsa minyewa asamazunze akazi awo. +Akapeza thanthwe pokumba manda zimatha bwanji? Zochitika kumanda nzambiri nthawi yokumba manda koma palibe nthawi yomwe adzukulu amakhaula kwambiri kuposa pamene apeza thanthwe dzenjelo lisadathe chifukwa sipakhala kusiya kuti akayambe pena. Uwu sumakhala ulesi, koma kuti ndi mwambo wake momwe zimayenera kukhalira. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi gulupu Mtwambwa wa ku Lilongwe yemwe akulongosola za mwambowu motere: Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mtwambwa: Kumakhala ngati kuwayesa azimu Mfumu, tiuzeni kuti ndinu yani? Ndine Gulupu Mtwambwa ya mdera la T/A Kalumba ndipo mtundu wathu ndi wa Achewa. +Mfumu, kumanda kumachitika zambiri adzukulu akamakumba koma chidandipatsako chidwi nchakuti akapeza mwala, mmalo mokwirira nkukumba pena amapitiriza. Kodi nchifukwa chiyani? Ndi mwambo umene uja, sangayerekeze kusiya dzenje loyambayamba nkuyambiranso lina chifukwa akhoza kukhala ndi mlandu waukulu mmudzi moti akhoza kulipitsidwa chindapusa chachikulu kapena kusamutsidwa kumene mmudzi atapanda kugonjera chigamulo cha akuluakulu. +Ndi mlandu wanji umenewu? Umenewu ndi mlandu wolowetsa mphepo mmudzi. Ife timakhulupirira kuti kuyamba kukumba dzenje nkulilekeza panjira kuli ngati kukumba dzenje koma osaikamo maliro, zomwe zimapangitsa kuti anthu azipululuka chifukwa mizimu yakwiya kuti mwainamiza kuti kukubwera mmodzi mwa ana awo. +Si zongokhulupirira izi nanu Achewa? Si zongokhulupirira, ayi, zimachitika. Ngakhale mutayenda kuno mpaka kufufuza mmanda simungapeze dzenje loyamba kukumbidwa kapena lomalizika kukumbidwa koma losaikamo mtembo. Zimenezi sizingatheke ndipo mfumu ya mmudzi momwe mungachitike zotere yokha imadziwiratu kuti ikhoza kukhala pamoto waukulu. +Nanga thanthwelo likakhala lalikulu? Basi adzukuluwo adziwa momwe achitire koma dzenjelo lipitirire basi mpaka lithe. Uthenga ukamabwera kumudzi kuti nyumba yatha kumanda, likhale kuti dzenjelo lakwanadi monga ndi momwe chikhalidwe chimanenera. +Si chilango kwa adzukulu chimenechi? Ayinso, palibe za chilango. Kodi tiwalanga ngati abweretsa zovuta ndi iwowo bwanji? Munthu akamati akulowa mgulu la adzukulu, amadziwiratu ntchito yomwe azikagwira kumeneko ndiye zonsezi amazidziwa kale, sizikhala zachilendo akakumana nazo. +Kapenatu mwina mumaona kuti malo angamathe msanga? Ndinu nkhakamira. Moti monse muja simukumvabe kuti timatsatira mwambo momwe umayenera kukhalira? Ifensotu tidakhalako adzukulu ndipo zimenezi tidakumanapo nazo, sikuti zayamba lero. Tidazipeza, zikupitirira ndipo zidzakhalako mpaka kalekale. +Nanga akakhala kuti akumba poti padaikidwa kale munthu? Apa pokha akhoza kufotsera nkuyamba pena, koma kuti mafumu adziwitsidwe ndipo akhale ndi umboni. Nzosavuta chifukwa mizimu singakwiye poti nayo imadziwa kuti alakwitsa, pamalopo padali kale nyumba ya wina. +Kolondoloza: Mwambo wokaona mwana wa Inkosi Kumayambiriro kwa chaka chino Angoni ochokera mboma la Mzimba adali chimwemwe tsaya kaamba ka kubadwa kwa mwana wamwamuna kubanja lachifumu la Inkosi ya Makhosi Mmbelwa ku Edingeni mboma la Mzimba. Mwa mwambo wa Angoni, mwanayu ndiye akuyembekezereka kudzalowa ufumuwu mtsogolo muno. MARTHA CHIRAMBO adacheza ndi Ndabazake Thole, mlembi wamkulu wa bungwe la Mzimba Heritage, yemwe akulongosola za momwe mwambowu udayendera motere: Ndakupezani wawa, ndamvetsedwa kuti mudapita kokaona mphatso ku Edingeni. Talongosolani, kodi mwambowu umayenda bwanji? Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Poyamba ndinene kuti koyambirira kwa chaka chino ife Angoni tidasangalala kwambiri ndi kubadwa kwa mwana wa mwamuna kwa Inkosi ya Makhosi Mmbelwa. Paja ufumu wa Agonifetu timaupitiriza ndi kubadwa kwa mwana wamwamuna kubanja lachifumu. Zikatero timakhala ndi chikhulupiriro chonse kuti ufumu upitirira ndipo timapemphera mwamphamvu kuti Mulungu amuteteze mwanayu. +Zikomo wawa, pitirizani kulongosola za mwambowu tsopano. +Mwanayu atabadwa, uthenga udatumizidwa kwa makhosi onse kapena nditi mafumu onse Achingoni ku Ekwendeni, Elangeni ndinso ku Emucisweni komanso midzi ina yonse. Uthengawu udatipezanso ife. +Mutalandira uthenga mudachitapo chani? Ife tidayamba kutsata ndondomeko yake yoti tikaone mwanayu. Sikuti umangodzuka lero ndi lero basi ndikukaona mwana, ayi, sititero. Ulendo wathu udali ndi zolinga zitatu monga kukamuona mwanayu, kukadziwa dzina lake, komanso kukapereka mphatso. Tidapempha kudzera kwa Inkosi Mpherembe yomwe ndi mlembi wamkulu wa khonsolo ya mafumu mwa a Mmbelwa. Kupatula apo, tidapemphanso kwa nduna ya komwe kulikulu ku Edingeni yomwe idatiloleza. Tidabwereranso kwa Mpherembe kukapemphanso chilolezo. +Nthawi yokaona mwana itakwana zidatani? Adatipatsa Inkosikazi Mtwalo kuti ndiyo itsogorere ulendowu. Pajatu ntchito yokaona mwana imaimira kwambiri azimayinu. Mwa ichi pagulu lathu abambo tidalipo ochepa kulekana ndi amayi. +Mwakambapo zokapereka mphatso. Mudanyamula mphatso zanji? Azimayi adatenga ufa, shuga ndi zina ndi zina zokhudza mwana, pomwe ife madoda tidanyamula kandiwo kake. Tidatenga mbuzi ngati ndiwo. Nanga ufa umayenda wopanda ndiwo zake? Tsopano mutafika ku Edingeni, mudayambira pati? Ife ngati madoda tidapereka malonje. Koma sitidakambeko kalikonse zokhudza kuona mwana. Pajatu tati ntchitoyi eniake enieni ndi amayi. Inkosikazi ndiyo idafotokoza cholinga cha ulendowo womwe tidapita a Mzimba Heritage ochokera ku Mzuzu, Mzimba boma komanso ku Lilongwe. Apa tidapereka mphatso. +Mudapereka mwana musadamuone? Talongosolani bwino pamenepa. +Iyo idali ya malonje chabe chifukwa ife Angoni tisadamuone mwana uja pamakhala mboni. Iyi ndi ndalama yomwe timaika mmbale yosonyeza kuti mtima wathudi tikufunitsitsa timuone mwanayu. Ndipo posakhalitsa amayi ndi agogo ake aakazi a mwana adatutuluka naye. Komatu tonse sitidamugwire kupatula inkosikazi chifukwa uyu ndi mwana wachifumu. +Zonsezi zimachitika musadadziwebe dzina? Eya. Udali mwambo wopatsa chidwitu ndi wosangalatsa kwambiri. Tidaperekanso mboni ina kuti tidziwe dzina ndipo makolo ake adatiuza kuti ndi Londisizwe lomwe likutanthauza mtetezi wa dziko kapena kuti mvikiliri wa charo mChitumbuka. Atangotchula dzina azimayi adalulutira komanso kuvina, ndipo ife a bungwe tidayamba tsopano kutumiza mauthenga palamya komanso paintaneti kwa abale ndi abwenzi za dzina. Dzina la mwana wa Inkosi ya Makhosi sumangouzidwa basi; pamakhala mboni ngati momwe zidachitikiramo. +Kodi akadabadwa mwana wamkazi chisangalalo chikadakhala chimodzimodzi? Pachikhalidwe chathu, akakhala mwana wamkazi zimapereka maganizo ndithu kwa anthu poganizira kuti ufumuwu salowa ndi munthu wamkazi. Koma akakhala mtsikana timadziwa kuti tsiku lina adzakwatiwa ndipo adzachoka pamudzi. +Adzinjata Kaamba Ka Mkazi Wamwini Chisoni chidaphetsa nkhwali. Ku Masasa, mumzinda wa Mzuzu mnyamata yemwe adalembedwa ntchito ya zomangamanga pakhomo pa bambo wina mderali mongomuthandiza atamumvera chisoni kaamba ka kuvutika, akumuganizira kuti adapezeka akuzemberana ndi mkazi wa njondayo. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Koma zachisoni-nkhaniyi akuti yatengera Joseph Nyirongo, yemwe adali wa zaka 23, kumanda atapezeka ali lende mumtengo wa paini pambuyo pomupezerera akuchita zadama mnyumba mwake ndi mkazi wa njondayo. +Nyamhone: Nachi chitsa cha mtengo wotembereredwa, pomwe adadzimangirira mwana wanga Wachiwiri kwa mneneri wa polisi mchigawo cha kumpoto, Cecilia Mfune, watsimikiza za nkhaniyi. +Mkati mwa sabatayi Msangulutso udacheza ndi mwini mkaziyo, Lovemore Luhanga, yemwe adanenetsa wamukhululukira atchalitchi atamukhazika pansi ndipo wati samusiya mkazi wake. +Luhanga, yemwe amaoneka mosatekeseka ndi mbiri yomwe yatchuka mderali, adati zili kwa mkazi wakeyu kusintha kapena ayi ati kaamba koti zomwe adachita zapangitsa munthu wina kuluza moyo wake. +Koma pachikhalidwe ndiwatumiza kaye kumudzi kuti akapitidwe mphepo yabwino; adzachita kubweranso, Luhanga adatero. +Bamboyu adati panthawi yodzikhwezayo Nyirongo adali atavala scumba ya akazi ake ya mtundu pepo (purple). +Mwana wanga wa zaka zitatu ndiye adaizindikira scumbayo chifukwa adapita ndi mnzake wa zaka 8 kukaona thupilo lili mumtengo ndipo adayamba kulozera mnzakeyo kuti amvekere amama bafwa, bali muchikhuni ataona scumbayo, Luhanga adatero. +Polongosola chomwe chidatsitsa dzaye, iye adati adayamba kumva mphekesera kuti mkazi wake akuzemberana ndi mnyamatayu mwezi wa November chaka chatha. +Luhanga, yemwe amachita bizinesi komanso ndi diraiva wa lole, adati mkazi wake wakhala akukana za chibwenzichi. +Amati sangachite naye chibwenzi chifukwa Nyirongo sankasamba; ndipo nanenso ndimakaikira chifukwadi adalibe ukhondo, iye adatero. +Koma Luhanga adati chibwenzichi chitafumbira, mkazi wakeyu adamupezera nyumba mnyamatayo komanso adayamba kumamupatsa ndalama zomwe amakatolera kubizinesi yawo yoperekera sopo wochapira ndi mafuta odzola. +Bamboyu adati Lachiwiri sabata yapitayo adalimba mtima ndi kumufunsa Nyirongo za mphekeserazo, zomwe ati mnyamatayo adakanitsitsa kwa mtu wa galu kuti sakudziwapo kanthu. +Apa akazi anga adatulukira ndipo nawonso adakanitsitsa za nkhaniyi. Ndidangowauza kuti ngati akuchitadi izi, tsiku la fote lidzawakwanira ndipo chomwe chitadzachitike sindidzalankhula zambiri. Tili mkati mokamba mayi anga adatulukira kudzatichezera ndipo nkhaniyi idathera pomwepo, adafotokoza motero Luhanga. +Iye adati patadutsa nthawi adatengana ndi mkazi wake komanso mwana wawo wa zaka zitatu kuwaperekeza mayi ake; koma mwadzidzidzi adazindikira kuti mkazi wake sali nawo paulendowu ndipo sikudziwika komwe alowera. +Luhanga adati adachoka koperekeza mayi ake nthawi ili cha mma 9 koloko usiku adatsekera ana mnyumba ndi kuyamba kufufuza komwe mkazi wakeyo adalowera chifukwa adali ndi K43 000 yomwe adatolera tsiku limenelo. +Iye adati nthawi ili cha mma 1 koloko mmawa anthu ena adamutsina khutu kuti mkazi wakeyo akamuyangane kunyumba kwa Nyirongo. +Nditafika ndidaima pawindo ndipo ndidamva awiriwo akulankhula. Apa ndidadzutsa eni nyumbazo kuti andikhalire umboni. Ndipo titagogoda, Nyirongo adatitsekulira koma adakanitsitsa zoti mkazi wanga adali mnyumbamo, Luhanga adalongosola motero. +Bamboyo adati adamulonjeza Nyirongo kuti ampatsa K10 000 ngati mkazi wakeyo sadali mnyumbamo. +Adanditsekulira ndipo nditangoti lowu, adandiponyera chikwanje pamutu chomwe chidandiphonya ndi kumenya feremu ya chitseko, kenaka adandimenya ndi chitsulo padiso ndi pamutu ndipo ndidagwa pansi. Apa nkuti mkazi wanga atathawira pawindo, bamboyo adatero. +Iye adati atadzuka adakuwa kuti: Wakuba! Wakuba! ndipo anthu ozungulira adamugwira mkaziyo nkuyamba kummenya. +Iye adati adaleretsa mkazi wakeyo mmanja mwa anthu okwiyawo ali buno bwamuswe ndipo adamupititsa kupolisi achisoni atamuponyera kachitenje. Luhanga adati adatengera mkazi wake kupolisiko pomuganizira kuti waba ndalama kaamba koti ndalama yomwe adali atatolerayo adali atamupatsa Nyirongo poti awiriwo amakonzekera zothawira ku Lilongwe. +Ndidatengana ndi apolisi kuti tidzamutenge Nyirongo, koma sitidamupeze. Ndidadzidzimuka kumva kuti wapezeka atadzimangirira, adatero Luhanga. +Pakadalipano mkaziyu akubindikira mnyumba kaamba ka manyazi ndi zomwe zidachitikazi chifukwa akatuluka anthu amangomulozaloza. Adakana kutuluka kuchipinda pomwe Msangulutso udafuna kumva mbali yake. +Mkucheza kwathu ndi mayi a wodzikhwezayo, mayi Nyamhone, iwo adati adazindikira kuti mwana wawoyo adadzimangilira nthawi ili mma 4 kololo mmawa wa Lachitatu ndipo sadasiye uthenga uliwonse. +A Nyamhone, omwe amagulitsa masuku, adati anzake ndi amene adawauza kuti mtengo womwe uli pafupi ndi nyumba yawo mukulendewera munthu. +Mayiwo adati mwana wawoyo, yemwe wasiya ana awiri ndipo banja lake lidatha mchaka cha 2010, adadzamugogodera cha pakati pa usiku ati kukangowaona. +Nyamhone adati Nyirongo adadzimangirira mumtengo wautali kwambiri ndipo pa nthawi yomwe adamuonayo adali asanamalizike koma kuti anthu sadakwanitse kukwera kuti amuombole. +Mwana wanga sadayambane ndi munthu aliyense ndipo sadandilongosolere kalikonse zokhudza mzimayi, a Nyamhone adatero. +Iwo adati koma adali okhumudwa ndi apolisi omwe ngakhale adauzidwa za ngoziyo mmawa adafika pamalopo 12 koloko masana ndipo thupilo sadalitengerenso kuchipatala ati kaamba koti lidali litayamba kale kufufuma. +TCC imema alimi a fodya kulembetsa Bungwe loyanganira za malonda a fodya mdziko muno la Tobacco Control Commission (TCC) lati alimi a fodya omwe sadalembetse nkulipira zitupa zawo alembetseretu kuti akhale nawo mkaundula wa alimi a fodya. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Chikalata chomwe bungweli latulutsa chati pofika mwezi wa June chaka chatha, alimi 29 861 ndiwo adali atalembetsa nkulipira zitupa zawo. +Alimi ayenera kulembetsa mkaundula nthawi isanathe Kutsika kwa chiwerengerochi kwapangitsa kuti bungwe la TCC liwonjezere nthawi yomwe alimi angakalembetsere ndi kulipira zitupa zawo zogulitsira fodya chaka chino mpaka pa 29 January 2016. +Malingana ndi chiwerengero cha alimi omwe alembetsa ndi kulipira ziphaso zawo, taganiza zoonjezera nthawi yolembetsera ndi kulipira kuti alimi omwe sadatero akhale ndi mpata. Alimi onse omwe sadalembetse kapena kulipira ziphaso zawo apangiretu nyengo yoonjezerayi, chatero chikalatacho. +Mkulu woyanganira za ubale wa wa bungweli ndi makampani kapena nthambi zina Mark Ndipita adati vutoli ladza kaamba ka zovuta zingapo monga zokhudza malonda a fodya. +Tikuganiza kuti mwina alimi ena akadali otangwanidwa ndi nkhani zokhudza malonda a chaka chatha komanso zochitika zina zosiyanasiyana monga mudziwa mmene nkhani ya fodya imakhalira, adatero Ndipita. +Iye adati ngakhale zinthu zili choncho, si kuti malonda a fodya a chaka chino asokonekera poti alimi a fodya amayendera mlingo wa fodya omwe amapereka a TCC ndipo umaonetsedwa pa chitupa. +Mkulu wa TCC Albert Changaya, adauza nyuzipepala ya The Nation kuti ogula fodya akunja atsitsa mlingo wa fodya yemwe agule chaka chino kuchoka pa makilogalamu 192.6 miliyoni chaka chatha kufika pa 177 miliyoni. +Changaya sadafotokoze chomwe chapangitsa kuti mlingowu utsike komanso ngati izi zikutanthauza kuti atsitsa mlingo a fodya pa zitupa za alimi pokakhomera. +Fodya ndi mbewu yomwe dziko la Malawi limadalira kwambiri pachuma chake koma pakatipa malonda a fodya akhala akukumana ndi zokhoma makamaka kuchokera ku bungwe la zaumoyo padziko lonse la World Health Organization (WHO) lomwe limachenjeza za mchitidwe wosuta fodya. +Pa malonda a 2015, dziko la Malawi lidapeza ndalama zokwana K189 biliyoni kuchoka pa K205 biliyoni mmalonda a mchaka cha 2014. +Lekani kulozanalozana, nyengo yasinthaMET Nthambi yoona za kusintha kwa nyengo ya Malawi Meteorological Services (MET) yati anthu adziwe kuti nyengo ikusintha ndipo aleke kulozana zala chifukwa palibe akuchititsa izi. +Mkulu wa nthambiyi Jolamu Nkhokwe adalankhula izi Lachitatu pamene nthambiyi imakumbukira tsiku la zanyengo. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Zikavuta choncho mmunda ena amaloza chala anzawo Nkhokwe adati nthambi yawo nthawi zonse imapereka uthenga wa momwe nyengo ikuyendera, koma akudabwa kuti ena akukhalabe moyo wachikale womaloza ena zizindikiro za kusintha kwa nyengo zikaoneka. +Ambiri sakudziwabe kuti pali kusintha kwa nyengo, dziwani kuti nyengo yasintha ndipo izi zikuoneka kudzera mnjira zambiri monga kusowa kwa mvula ndi kusefukira kwa madzi. +Anthu agwiritsire ntchito uthenga womwe tikuwapatsa kuti atsatizire bwino za kusintha kwa nyengo. Tsiku lililonse tikumatulutsa uthenga wa momwe nyengo ilili koma tikudabwa kuti ena akukhala moyo wachikale, adatero Nkhokwe. +Kulankhula kwa Nkhokwe kukudza pamene mdziko muno anthu okalamba akukwapulidwa, ena kuwapha kumene powaganizira kuti akutseka mvula. +Ku Chiradzulu mwezi wathawu ndiye anthu 7 adaothetsedwa moto masanasana ndipo adawasiya atalonjeza kuti mvula ibwera. +Nkhoswe adati izi ndi zachisoni chifukwa palibe amene angatseke kapena kumasula mvula ndipo wapempha anthu kuti azitsatira zomwe nthambi yawo ikutulutsa kukhudzana ndi momwe nyengo ikhalire. +Malawi ndi limodzi mwa maiko amene akhudzidwa ndi kusintha kwa nyengo moti mvula chaka chino yagwa mwanjomba kupangitsa kuti ena asaphulemo kanthu mminda yawo. +Bwalo lilanga mphunzitsi wochimwitsa mwana Bwalo la milandu la majisitireti la Mzuzu lapeza mphunzitsi wina wolakwa pamlandu wochimwitsa mtsikana wosakwana zaka 16, komanso kupereka mankhwala ochotsera pathupi pomwe adampatsa. Bwaloli likuyembekezeka kupereka chilango chake mawa pa 22 February. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Lachinayi sabata yatha bwaloli lidamva kuti Mtendere Phiri, wa zaka 31, yemwe kwawo ndi ku Bembeke, T/A Kachindamoto, mboma la Dedza, adayamba kugonana ndi mwanayu mwezi wa April chaka chatha. +Bwaloli lidamva kuti Phiri, yemwe amaphunzitsa pasukulu ina yapulaimare ku Ekwendeni mboma la Mzimba, adanyengerera mtsikanayu kuti akakana chibwenzi, asiya kuphunzitsa pasukulupo ndipo apita kwina. +Izi zidamukhudza mtsikanayu ndipo posafuna kuti mphunzitsiyo achoke, adamulola ndipo ankapita kunyumba kwake mkazi wake akapita ku Mzuzu kwa mayi ake, adawerenga majisitireti Agness Gondwe. +Apatu nkuti Phiri yemwe adavala malaya ofiira, ali wera mchitokosi cha bwalo la milandu, naye mkazi wake ali poteropo kumvetsera majisitiretiyu. +Ndipo iye adapitiriza kuti malinga ndi umboni womwe udaperekedwa mbwalolo masiku apitawo, awiriwa ankachita zadamazi kuchipinda kwa mphunzitsiyu. +Gondwe adati mtsikanayu adauzanso bwalolo poperekera umboni wake kuti zadamazi zidachitika kosawerengeka ndipo Phiri adamuuza kuti akadzadutsitsa mwezi osasamba adzamudziwitse msanga. +Iye adati mwezi wa July msikanayu adaima ndipo atamudziwitsa mphunzitsiyu, sadachedwe koma kumupatsa mapilitsi awiri a Brufen komanso a Bactrim zomwe sizidaphule kanthu chifukwa pathupipo sipadachoke. +Majisitiretiyu adati apa mtsikanayu adapita kutchuthi mumzinda wa Mzuzu komwe pobwerera mmwezi wa September mayi ake adamuzindikira kuti adali ndi pathupi. +Iye adati mayi a mtsikanayu adamuuzitsa kuti asachotse mimbayo, koma izi sizidathandize chifukwa atakumananso ndi mphunzitsiyo adamuuza kuti ngati atasunge pathupipo zake zida. +Malinga ndi umboni womwe udaperekedwa mbwalo lino, Phiri adamuuza mtsikanayo kuti apite naye kuchipatala cha Banja La Mtsogolo (BLM) akamuchotse, koma atakana adakagula mankhwala asanu ndi anayi kuchipatalachi, adatero Gondwe. +Mtsikanayu atamwa, pathupipo padachokadi pakati pa usiku ndipo adakataya zomwe zidatulukazo mchimbudzi. +Koma madzi adachita katondo pomwe mtsikanayu adayamba kugudubuzika ndi ululu wa mmimba ndipo adaulula kwa mayi ake kuti mphunzitsiyo ndiye adali mwini nkhaniyi. +Apa adathamangira naye pachipatala chachingono cha mderali komwe adamutumiza kuchipatala chachikulu cha Mzuzu Central komwe adamuchotsa zotsalira. +Ndipo mayi a mwanayu molimbikitsidwa ndi a mabungwe adakamangala kupolisi komwe adamutsekera Phiri pa September 23 chaka chatha. +Christon Ghambi, yemwe akuimira mphunzitsiyu, adaseketsa bwaloli pomwe adalipempha kuti limuganizire phiri posampatsa chilango chokhwima poti adapereka mankhwala ochotsera pathupiwo kuti tsogolo la mwanayu lisaonongeke. +Mutharika achenjeza akamberembere Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika wasonyeza kuti amatsatira ukamberembere omwe umachitika mkatikati mwa malonda a fodya ndipo wachenjeza ogulitsa ndi ogula kuti sakufuna nyansizi chaka chino. +Mutharika adapereka chenjezoli potsegulira msika wa fodya wa chaka chino ku ku Kanengo mumzinda wa Lilongwe Lachitatu lapitali. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Iye sadasiye mbali podzudzula ndi kuchenjeza onse okhudzidwa mmalondawa ponena kuti ogula ali ndi chisimo chosintha mawanga mkatikati mwa malonda pomwe ogulitsa adawadzudzula kuti amachulutsa ukamberembere poika zitsotso mmabelo awo. +Inu makampani ogula fodya ndikuchenjezeni pano. Tsiku loyamba, mumagula fodya pamitengo yomwe idakhazikitsidwa koma kenako nkusintha mawanga mkatikati mwa msika. Zimenezi sitikuzifuna chaka chino, adatero Mutharika. +Iye adati mchitidwe wotere umayambitsa mikangano pakati pa ogula fodya ndi alimi mpaka msika kumasokonezeka chifukwa cha kusamvana. +Mutharika adatembenukiranso kwa alimi nkuwadzudzula kuti achepetse ukamberembere woika zitsotso mmabelo ndi cholinga chopusitsa makampani ogula fodya kuti mabelo awo azilemera pomwe muli fodya wochepa kapena woipa. +Inuso alimi ndikuchenjezeni pakhalidwe loika zinthu zosayenera mmabelo a fodya. Khalidwe limene lija ndilo limapangitsa kuti makampani azibweza fodya wambiri pamapeto pake mumakhala ngatimudagwira ntchito yopanda malipiro, adatero Mutharika. +Iye adati ali ndi chiyembekezo kuti malonda a fodya ayenda bwino chaka chino poyerekeza ndi zaka za mmbuyo pomwe kumakhala kusamvana kwakukulu pakati pa alimi andi makampani ogula fodya, makamaka pankhani ya mitengo ndi maonekedwe a fodya. +Fodya wa chaka chino ayamba kumugula pamtengo wa $0.80 (pafupifupi K552) pa kilogalamu pomwe kusiyana ndi chaka chatha pomwe adayamba ndi $2.32 (pafupifupi K1, 044 pa kilogalamu potengera mphamvu ya kwacha panthawiyo). +Izi zili chonchi, bungwe la Tobacco Control Commission (TCC) lati ndi lokhudzidwa ndi kuchuluka kwa fodya yemwe akubwezedwa potengera tsiku lotsegulira msikali pomwe mabelo 30 pa mabelo 100 alionse amabwezedwa. +Mkulu wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) Alfred Kapichira-Banda adati nzodabwitsa kuti kwacha yayamba kukwera mphamvu pomwe alimi akugulitsa fodya pomwe adagula zipangizo mokwera kwacha itagwa. +Chilala chavuta maboma ambiri Nduna ya zamalimidwe ndi chitukuko cha madzi, Dr Allan Chiyembekeza, wati pakhala msonkhano wounikira momwe ngamba yakhudzira anthu makamaka mchigawo cha kummwera. +Chiyembekeza adanena izi msabatayi atayendera madera omwe ngamba yavuta mmaboma ena a dziko lino. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ulendo wa Chiyembekeza udali wachisoni chifukwa maboma ena alimi sadabzale, ena chimanga chafota pamene madera ena sichidamere. +Gojo: Chimanga chikamasula popanda mvula sichingabereke Malinga ndi malipoti a mmaboma amene aperekedwa ku unduna wa zamalimidwe, mmaboma a Phalombe, Chiradzulu, Nsanje, Chikwawa, Neno ndi Mwanza ndi komwe kwavuta kwambiri chifukwa cha kusowa kwa mvula. +Mwachitsanzo, boma la Phalombe lalandira mvula masiku 8 okha. Malinga ndi lipotilo, pofika Lolemba pa 25 January nkuti mvula yozama ndi mamilimita 130.6 okha itagwa. Nthawi ngati yomweyo chaka chatha nkuti bomalo litalandira mvula kwa masiku 27 ndipo idali itazama ndi mamilimita 663. +Mkulu wa zamalimidwe mbomalo, Osmund Chapotoka, wati chifukwa cha kuchepa kwa mvula, alimi amene adabzala koyambirira, chimanga chawo chafota pamene amene adabzala kumapeto, chimanga chawo sichidamere. +Ngakhale mvula itagwa lero chimanga chimenechi sichingapulumuke. Apa ndiye kuti alimi ayambiranso kubzala, adatero Chapotoka. Tili ndi madera amene kumavuta mvula chaka chilichonse monga ku Kasongo, koma pano ndi madera omwe kumagwa bwino mvulawo kuli gwaaa! Alimi onse akulira. +Nako ku Thyolo, ndiye angolandira mvula kwa masiku 14 yochuluka ndi mamilimita 199.9 basi. Nthawi ngati yomweyi chaka chatha nkuti bomali litalandira kale mvula kwa masiku 22 yomwe idali yozama ndi mamilimita 558.2. +Kumenekonso, malinga ndi mkulu wa zamalimidwe, Raphael Mkisi, zinthu zasokonekera. +Chiyembekeza: Tikumana Mvula idasiya chimanga chitangoyamba kupota. Yadula kwa sabata ziwiri ndiye ngakhale yayambiranso pano, sichingabereke ndipo alimi akuyenera abzalenso, adatero Mkisi. +Ku Mulanje mvula yangogwa masiku 15 yozama mamilimita 284.8. Nthawi yonga yomweyi chaka chatha nkuti atalandira mvula kwa masiku 32 yozama ndi mamilimita 934.9. +Ku Neno ndiye angolandira mvula ya mamilimita 150.5 yomwe yagwa kwa masiku 8. Nthawi ngati yomweyi chaka chatha, bomali lidali litalandira mvula ya mamilimita 806.5 kwa masiku 24. +Chiyembekeza akuti maboma a Balaka, Nsanje, Chikwawa, Ntcheu, Machinga, Chiradzulu ndi ena ali mmavuto onga omwewa ndipo zikuchititsa mantha. +Ili si vuto la munthu, Namalenga ndiye akudziwa zonse ndipo sitikudziwa kuti watikonzera zotani chifukwa palibe boma lomwe lili ndi nkhani yabwino, adatero Chiyembekeza. +Kuchigawo cha kumpoto lipoti lofotokoza momwe zinthu zilili silidaperekedwe kuboma koma ndunayi yati posakhalitsapa lipotilo lituluka pamene iyo ipitenso kukayendera mmaboma ena. +Tilibe komwe tikulandira mvula mokhazikika, chaka chino tikuyenera kusamala kwambiri chifukwa tilibe chiyembekezo kuti tipeza chakudya chokwanira malinga ndi momwe mvulayi ikugwera, adatero Chiyembekeza. +Komabe ndunayi yati kupatula kuti boma likhala pansi kukambirana za chomwe achite, alimi akuyenera ayambe kubzala mbewu zina zosalira mvula yambiri. +Ngati mvula itabwera, tisalimbanenso ndi kuthira feteleza chimanga chomwe sitikololapo. Ndi bwino timusunge fetelezayo kuti tikagwiritsire ntchito paulimi wamthirira. +Alimi akonzeke kubzala mbewu zina monga chinangwa, mapira, mchewere, mbatata ndi mbewu zina zosafuna madzi ambiri ngati mvula yagwa kudera kwawo, adatero Chiyembekeza. +Iye adati si dziko lokha la Malawi lomwe lakumana ndi chilalachi komanso maiko monga a South Africa, Lesotho kudzanso Zambia nawo ali pamoto monga zilili kuno. Chiyembekeza adati boma liyesa kupeza njira zoti lithandizire anthu. +Si vuto la mvula lokha, maboma a Phalombe ndi Mulanje ntchemberezandonda nazo zikuteketa mmera womwe wangomera. +Undunawu ukuyembekezera kutulutsa lipoti lomwe lifotokoze momwe zinthu zilili mdziko muno ukamaliza kuyendera maboma onse. +Pamenepo ndipo padziwikenso momwe chaka chino anthu akololere ngakhale Chiyembekeza wataya chiyembekezo chokolola dzambiri. +Anthu oposa 3 miliyoni mdziko muno ndiwo akutuwa ndi njala ndipo boma layamba kale kugawa chakudya mmaboma ena. +Koma monga akulirira Nyakwawa Gojo ya mboma la Mulanje, chaka chino kulira kulipo chifukwa anthu alibe chakudya pamenenso chiyembekezo chokolola chachoka. +Onani mmunda mwanga muno, chimanga chonse chamasula pamene mvula kulibe. Ngakhale itabwera lero palibe chomwe chingachitike. Mulungu amve kulira kwathu, adalira Gojo. +Anatchezera Akumandiipitsa Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Zikomo agogo, Ndili ndi chibwenzi ndipo makolo akudziwa ngakhale kuti ndi mwamphekesera chabe. Nthawi ina bambo ake (osati omubereka) amafuna kumugwiririra ndiye akumandiipitsa dzina kwa mayi ake, koma iwo sakutekeseka ndi izi. Ndili ndi mantha, nditani pamenepa agogo? Ine GK, Lilongwe. +GK, Wati uli ndi mantha, mantha ake otani? Sindikuonapo chifukwa choti uzikhala ndi mantha pamene sudalakwire munthu aliyense. Ndiye iwe ukuchita mantha ndi ndani? Ngatidi ukunena zoona kuti bambo omupeza a mtsikanayo adafunadi kumugwiririra, bwenzi lakolo adachitapo chiyani zitachitika zimenezo? Kodi mayi a mtsikanayo nkhaniyi akuidziwa? Ngati akuidziwa adachitapo chiyani? Ndikufunsa mafunso onsewa chifukwa ndi mlandu waukulu kugwiririra kapena kufuna kugwiririra ndipo munthu wopalamula mlandu wotere amayenera kulangidwa kundende malinga ndi malamulo a dziko lino. Munthu wotere ngosafuna kumusekerera. Ndibwerere kunkhani yako yoti uli ndi mantha. Ngati umamukonda zoona mtsikanayo pitiriza kutero chifukwa tsiku lina udzakhala mpulumutsi wake kwa bambo womupezayo mukadzakhala thupi limodzi. Mwina mayi ake sakutekeseka ndi zokuipitsira dzina lako chifukwa akudziwa choona chenicheni, maka pankhani yoti amuna awo amafuna kugwiririra mwana wawo, koma akukhala chete chifukwa akuopa kuti angawasiye banja. +Akuti tibwererane Gogo wanga, Ndinali pachibwenzi ndi mtsikana wina kwa miyezi isanu ndi umodzi. Pamene timati tipange ukwati mwezi wotsatira iyeyo adathetsa chibwenzi ndi kutengana ndi wina. Patatha miyezi iwiri adabwera ndi kudzandipepesa ati tibwererane koma akwathu akukana. Kodi nditani pamenepa? NF, Dedza. +NF, Mvera malangizo a makolo ako kapena akwanu amene akuti usayerekeze kubwererana naye chifukwa zimene akukulangizazo ndi zoona. Mawu a akulu amakoma akagonera, ukanyalanyaza udzalirira kuutsi tsiku lina. Iye adathetsa chibwenzi pakati pa iwe ndi iye ndipo adakwatiwa ndi wina kenaka patha miyezi iwiri uyo akubwera poyera ali undikhululukire, tibwererane. Alibe manyazi! Chavuta komwe adakakwatiwako ndi chiyani? Chilipochilipo. Ndiye iwe ukavomereza zoti mubwererane udzaoneka wombwambwana; wodya masanzi. +Ndimukhulupirire? Agogo, Ndili pachibwenzi ndi mnyamata wina wake. Ndakhala naye zaka zinayi. Chaka chino adakaonekera kwathu koma ineyo akundikaniza kuti ndikaonekere kwawo. Ndikamufunsa kuti akundikaniza chifukwa chiyani sayankha zogwira mtima koma ndikamufunsa za ukwati amavomera ndi mtima wake wonse. Ndimukhulupirire? Ine Fannie, Blantyre. +Fannie, Zikomo kwambiri pondilembera. Funso lako ndalimva ndipo ndiyesetsa kuti ndikuthandize mmaganizo. Wati mnyamatayo adakaonekera kwanu chaka chino kutanthauza kuti walimba mtima za ukwati. Poti miyambo kusiyana, kodi kwanu mtsikana amakaonekeranso kwa makolo a mwamuna? Kwa ine izi nzachilendo chifukwa kwathu kulibe zotere; mwamuna ndiye amakonekera kwawo kwa mkazi osati mtsikana. Ndiye ngati kwanu kuli mwambo woti mtsikana naye amakaonekera kwawo kwa mwamuna ndipo iye akukuletsa, ndiye kuti chilipo chomwe akubisa, mwina nkutheka kuti ali ndi mkazi kale ndipo akuopa kuti umutulukira. Koma ngati mwambo umenewo kulibe, palibe chifukwa choti iwe ukaonekere kwawo pokhapokha makolo a mnyamatayo atakhala ndi chidwi choti adzakuone. +Mlonda anjatidwa kaamba kosolola Pamene kampani ya Inovantis mboma la Machinga imanyadira kuti izigona tulo tozuna chifukwa yalemba ntchito Ibrahim Justin, wa zaka 23, ngati mlonda woteteza katundu wawo ku ndipsi, kampaniyi sinadziwe kuti yatuma galu kumalondera nyama ya mbuzi yowotcha kale. +Wapolisi wotengera milandu kukhothi pa Liwonde Police Post, Ezekiel Kalunga, adauza bwalo la milandu la Liwonde kuti pa April 19 chaka chino akuluakulu a kampani ya Inovantis adakagwada kupolisi kukadandaula kuti chipangizo chopanga mphamvu ya magetsi kuchokera kudzuwa (solar panel) chidasowa pakampanipo. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kafukufuku woyangana chipangizochi ali mkati mkulu wa alonda pakampanipo adakumana ndi munthu wina atanyamula chipangizocho, chimene adachizindikira kuti ndi cha kampani yawo. +Alonda onse adatengeredwa kupolisi ndipo atapanikizidwa ndi mafunso kuti adazembetsa chipangizocho ndani, Justin adavomera kuti ndiyeyo adasolola. +Kalunga adapempha khothi kuti limuthyape Justin ndi chilango chachikulu popeza khalidwe lakelo ndi lothawitsa anthu, makamaka a maiko akunja monga Inovantis, kudzakhazikitsa bizinesi zawo mdziko muno. +Popereka dandaulo, Justin adapempha bwalo kuti limupatse chilango chochepa popeza iye ndi nsanamira ya banja lake. +Woweruza milandu, Esther Phiri, adagwirizana ndi Kalunga ponena kuti khaliwe lakuba limabwezeretsa chitukuko mmbuyo kotero adamugamula kuti mlondayo akaseweze ndende kwa zaka ziwiri akugwira ntchito yakalavulagaga. +Justin amachokera mmudzi wa Kaudzu mdera la mfumu yaikulu Sitola mbomalo. +Apolisi adalakwa pomanga aphungu Katswiri wina wa za malamulo ndi anthu ena othirapo ndemanga agwirizana ndi bungwe la Malawi Law Society (MLS) ponena kuti kumanga phungu wa Nyumba ya Malamulo pomwe mkhumano wa Nyumbayo uli mkati ndi kulakwira malamulo a dziko lino. +Mphunzitsi wa zamalamulo kusukulu yaukachenjede ya Chancellor College, Edge Kanyongolo, wanenanso kuti kumanga anthu pogwiritsa ntchito mauthenga a pafoni nkuwaphwanyira ufulu wawo wokhala ndi chinsinsi. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kanyongolo adanena izi msambatayi apolisi atagwira aphungu awiri ena a Nyumba ya Malamulo a chipani cha MCP, Peter Chakhwantha ndi Jessie Kabwila, ndi mkulu wina wa chipanichi, Ulemu Msungama powaganizira kuti amakambirana zogwetsa boma la Peter Mutharika pamauthenga a palamya otchedwa WhatsApp. +Izi zitangochitika, bungwe la maloya la Malawi Law Society (MLS) lidati apolisi adaphwanya lamulo pomanga aphunguwo masiku a zokambirana zawo asanathe. +Gawo 21 la malamulo oyendetsera dziko lino limati aliyense ali ndi ufulu wokhala ndi chinsinsi. Lamuloli limaletsa kusechedwa opanda chikalata cha boma, kulandidwa katundu ngakhalenso kuwerengeredwa kalata komanso nkhani zonse zokhudza mafoni, adatero Kanyongolo. +Iye adati umboni wotengedwa popanda chilolezo wotere suloledwa kukhoti ndipo ngati wina angapereke umboni wotere, akhoza kusumiridwa. +Koma zikhoza kuvuta ngati mmodzi mwa amene amakambirana nawo izi ndiye adakapereka mauthengawo kupolisi, adatero Kanyongolo. +Mpungwepungwe udayamba Lamulungu pomwe apolisi adamanga Msungama pomuganizira kuti akukhudzidwa ndi nkhaniyo pomwe Chakhwantha ndi Kabwila samadziwika komwe adali. +Koma Lolemba pamene msonkhano wa aphunguwo udayamba, apolisi adatchinga zipata zotulukira ku Nyumbayo koma sadathe kugwira aphungu awiriwo. Kabwila adamugwira akuti azithawira kumaofesi a kazembe wa dziko la Germany pomwe Chakhwantha adakadzipereka yekha kupolisi Lachiwiri. +Kanyongolo adati malamulo a dziko lino salola kumanga phungu pomwe mkhumano wa Nyumba ya Malamulo uli mkati. +Ndime 60(1) ya malamulo imanena kuti phungu ali ndi chitetezo choti sangamangidwe panthawi yomwe akupita, kuchokera kapena pomwe ali ku Nyumba ya Malamulo, adatero Kanyongolo. +Naye mphunzitsi wotchuka wa za malamulo ku Cape Town mdziko la South Africa, Danwood Chirwa, adapherapo mphongo ponena kuti aphungu akangoyamba kukumana amakhala otetezedwa pankhani yomangidwa ngakhale kuti sali mNyumbamo. +Malamulo amati aphungu sayenera kumangidwa zokambirana zikatsegulidwa chifukwa amakhala otetezedwa. Zokambirana zingatenge nthawi yaitali bwanji chitetezochi chimakhalapo koma akhoza kudzamangidwa zokambirana zikatsekedwa, adatero Chirwa. +Mpungwepungwe wa Lachiwiriwo udachititsa sipikala wa Nyumba ya Malamulo Richard Msowoya kuimitsa msonkhano wa aphungu atamasulira kumangidwa kwa aphunguwo ngati kuchepetsa mphamvu za Nyumbayi. +Zokambirana ziyamba zaima mpaka boma lititsimikizire za chitetezo chathu ngati aphungu a Nyumba ya Malamulo, adatero Msowoya. +Koma mkulu wa apolisi Lexton Kachama adati apolisi sadalakwe pomanga atatuwo ndipo adati akadafufuza nkhaniyi. +Sitidachite kutumidwa ndi andale. Anthuwo sitidawazenge mlandu wofuna kuukira boma chifukwa tidangofuna kumva mbali yawo. Ntchito yathu ngati apolisi nkusungitsa bata ndipo izi timachita mwa ukadaulo wathu, adatero Kachama ngakhale sadafune kunena momwe adapezera mauthenga a foni za eni ake. +Mpungwepungwewu udayamba sabata yatha kumkhumano wa komiti yoona za mmene zinthu zikuyendera mdziko ya Public Affairs Committee (PAC) mumzinda wa Blantyre komwe nthumwi za boma ndi zotsutsa boma zidasemphana Chichewa pankhani yoti Mutharika ayenera kutula pansi udindo wake ngati mtsogoleri wa dziko lino ati kaamba kolephera kupeza mayankho a mavuto a zachuma ndi kusowa kwa chimanga mmisika ya Admarc. +Kusemphanako kudabuka nthumwi zotsutsa boma zitatemetsa nkhwangwa pamwala kuti Mutharika atule pansi udindo kaamba kolephera kuyendetsa bwino zinthu. +Nkhani yomwe idavuta kwambiri ndi ya kayendetsedwe ka chuma ndi njala yomwe yasanduka mutu wa nkhani pafupifupi paliponse mdziko muno maka pakusowa kwa chimanga mmisika ya Admarc. +Zipanizi zidapereka malire a masiku 30 kuti boma litumize chimanga mmisika ya Admarc kapena litule pansi udindo kuti ena omwe angakhale ndi njira zothetsera vutoli atenge phamvu zoyendetsa boma. +Pamkhumanowu, aphungu akuyembekezeka kukambirana za momwe chuma chikuyendera, nkhani ya njala, nkhani yokhudza ufulu wolemba ndi kufalitsa nkhani ndi mitu ina yomwe idatsalira pazokambirana za ndondomeko ya chuma cha 2015/16. +Nkhani yokhudza ufulu wa atolankhani yakhala ikuvuta ndipo ndi imodzi mwa nkhani zikuluzikulu zomwe zidabwerera pamkhumano wa ndondomeko ya chuma womwe wapitawo ndipo bungwe la atolankhani ndi maiko ena kudzera mwa akazembe awo adadzudzula kuponderedzedwa kwa nkhaniyi. +Pulofeti Meja wagawa dziko pawiri Mudamvapo inu zakuti ambiri amadana ndi mneneri kwawo komwe. Izi zikupherezera masiku omaliza ngati ano. +Abale anzanga, zidaliko pa Wenela tsiku limenelo pomwe adafika woimba wina, akuti David. Nyimbo yake idali yachilendo ndithu, ati Osaopa ya David kunyoza mkulu wina wotchedwa Meja. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Gawo lina la nyimboyo, imene ena atulutsa Part 2 akuti Rebirth ikumadutsa motere: Ndikumva ziwanda zako zikuti Eeh! Papa game yalakwa papa Ufiti Ndikupukusa legeni yanga kumwala Ndine mwana wa Mulungu sungandiphe ndi mankhwala Ukamaimvera nyimboyi, ikumamveka ngati ukuona uja Davide wa mbuku lopatulika, inde uja adapha chiphona Goliyati ndi mwala, yemwenso adapha mkango umene unkafuna kudya nkhosa zomwe amaweta! Uyu mneneri Meja ndithu wagawanitsa anthu pano pa Wenela. Aliyense lero akukhala wodana naye kapena womukonda. Amene akuchuluka sitikudziwa. Chomwe ndikudziwa nchakuti mneneriyu ulusi amauswa, adatero Abiti Patuma. +Kalekale ndinkakonda kuwerenga za Emmanuel N uja wa sataniki amene adalapa machimo ake. Iye ankakamba za ndalama, zovala, akazi okongola ndi zina zotero zochokera pansi pa madzi, adatero Gervazzio, uku akuika nyimbo ya Piksy yatsopano ya Angozo. +Nsanje idakula zedi pano pa Wenela. Ukalemera, ati sataniki. Ukakalamba, ati ufiti. Ukachita bwino ati walowa kashigeti. Uyu mneneri Meja mpatali. Go deep, real deep, mama, adatero Abiti Patuma. +Mawu ake ali mkamwa adatulukira mneneri Meja. Adali atagwirira mmwamba, miyendo ili lende. +Madzi ndi mpweya chopepuka nchiyani? Kodi iye amene akuyenda pamadzi ndi amene akuyenda mumpweya, shasha ndi uti? adafunsa mneneri Meja, mbale wa mneneri Bashir. +Mneneri, kodi uneneri uli ngati matenda a pamphasa? adafunsa Abiti Patuma. +Koma Abiti Patuma amadziwa kuphinduka ngati nyengo. Wasintha kale? Matenda a pamphasa, ndiye ati? Tell me more before the seed you plant bears you some miraculous bucks, adatero Mneneri Meja, inde mbale wa mneneri Bashir. +Matenda opatsirana pogonana. Uneneritu masiku ano uli ngati matenda a pamphasa: chindoko, chinzonono, mabomu ndi zina zotero. Ngati mwamuna awatenga, naye mkazi amugwira, adayankha Abiti Patuma. +Ziii wakeyo! Nanga taonani mneneri mayi Meja adati wina adapemphera ndipo adapeza mwayi wa katapira. Koma kuti akabweze ndalama kwa mwini banki ya ku Chinayo, adamuuza kuti ayi, kulibe ngongole. Miraculous bucks imeneyo. Bwanji mukunamiza mtundu wanga? adafunsa Abiti Patuma. +Sindikuona chachilendo. Kalelo aneneri ngati ine tinkalasidwa miyala mpaka kufa. Mwaiwala Sitefano? Ndine Meja Sitefano, adayankha munthu wa Mulungu. +Kukamba za Moya Pete! Mkuluyu wanyangala. Pajatu iyi ndi sabata imene Mfumu Mose idapita kumtsinje kukazula chinangwa. Ena amati mfumuyo idalowera kumtsinjeko pa 5 April, ena 6 enanso 7. +Miyezi ikutha osalandirandalama za mthandizi Akugona ndi njala, ena akudya nyanya (mizu ya mitengo yoyanga) pamene akudikirirabe ndalama zawo za ntchito ya mthandizi yomwe zatenga nthawi. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Tamvani yapeza kuti maboma ena, anthu atha miyezi iwiri asadalandirebe ndalama zawo chigwirireni ntchito mu November pamene maboma ena alandira kumene. +Kusowa kwa ndalama zogulira ufa kwadzetsa kudya nyanya Koma mneneri wa nthambi yoyendetsa ndondomekoyi ya Local Development Fund (LDF) Ina Thombozi wati chomwe akudziwa nchakuti ndalamazi zidatumizidwa mmaboma kuti anthu alandire ndiye oyenera kulankhulapo ndi amene akuyendetsa ndondomekoyi paboma. +Kuchedwa kwa ndalamazi kwachititsa kuti anthu ayambe kudya mizu ya nthochi pamene ena akudya nyanya zomwe ena zikuwatupitsa kapena kutsekula mmimba. +Boma lidakhazikitsa ndondomekoyi kuti ithandize anthu ovutika. Anthuwa amalandira K600 patsiku akalima msewu koma ndalamazo amayenera kulandira pakadutsa masiku 12 chiyambireni kulimako. +Kumayambiriro a January, nthambi ya LDF idatulutsa uthenga kuti ndalama zokwanira K5.4 biliyoni zatumizidwa mmakhonsolo onse kuti anthu ayambe kugwira ntchitoyi ndipo anthu 450 000 okha ndiwo apindule ndi thandizoli mdziko lonse. +Monga akufotokozera gulupu Mpochela wa kwa T/A Phambala mboma la Ntcheu, anthu ake atha miyezi iwiri asadalandire ndalamazo chilimireni msewu. +Adayamba kalekale kulengeza za tsiku lomwe tilandire ndalamazo. Tidayambatu kulima mu November koma mpaka lero sitidalandire ndalama, adatero Mpochela. +Mmudzi mwa Mpochela tsopano muli nkhawa kuti wina angamwalire ndi njala chifukwa anthu akusowa chakudya. +Charles Chinangwa wa mwa gulupu Mpochela mbomalo amene ali ndi ana 8 akuti akugonera nyanya kapena mizu ya nthochi pamene alibe pothawira. +Pocheza ndi Tamvani uko mphika wa nyanya uli pamoto, Chinangwa adati boma liwapatse ndalama zawo kuti agulire chakudya. +Takhala tikudya nyanya kuyambira mu October chaka chatha. Panopanso nyanya zikusowa ndipo sitikudziwa kuti tilowera kuti. Ena osemphana nazo magazi akutupa nazo pamene ena zikuwatsegula mmimba, adatero Chinangwa. +Gulupu Mpochela akuti wakhala akupita ku ofesi ya DC mboma lawo koma palibe thandizo lomwe alandira kufika pano. +Ndidakafikanso kwa phungu wathu, akungoti apereka dandauloli ku boma koma kuli ziii, anthu anga akuvutika ndi njala moti ena ayamba kutupa, chakudya kulibe koma anthu adagwira kale ntchito ya mthandizi, adatero Mpochela. +Yemwe amayendetsa za mthandizi mbomalo Kondwani Mjumira wati anthu ena sadalandire monga kwa Phambala ndi madera ena koma anthuwa alandira posakhalitsa. +Ndalama zilipo, ena alandira kale moti kumene mukukunenako akulandira sabata imeneyi, adatero pamene adatinso akuyenera kufufuza ngati anthu ena sadalandire ndalama kuyambira November. +Maboma ena monga Neno, Phalombe, Mulanje, Thyolo ndi Nsanje anthu akuti sadalandire ndalama zawo pamene ena. +Tidakhulupirirana tsiku loyamba Chikondi chidayambira kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College komwe Dennis Lupenga akuti atakumana ndi Sheila Chimphamba mchaka cha 2013 pomwe onse amachita maphunziro, adakhulupirirana tsiku lomwelo. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Awiriwa adamaliza maphunziro awo ndipo Sheila amagwira ntchito muofesi ya mapolojekiti komanso ndi mkonzi wa mapologalamu kuwayilesi ya Zodiak pomwe Dennis ali ndi kampani yake ya zamakina a Internet. +Dennis akuti ubale wa awiriwa udayamba pa 9 April chaka chokumanacho Awiriwa tsopano ndi thupi limodzi cha 2013 iye atauza njoyelo mwachindunji kuti akufuna kumukwatira osati za chibwenzi monga momwe anthu ambiri amayambira. +Ndidalibe nthawi yotaya nkumati ndili pachibwenzi chifukwa Sheila adandigwiriratu mtima ndipo ndidalibeso nthawi yoti ndimuone kaye ayi, adatero Dennis. +Iwo akuti ngakhale uku kudali kusukulu, mmaganizo mwawo mudalibe za chibwenzi koma kuti akungoyembekezera tsiku lodzalowa mbanja ndipo panthawi yonseyi sadasiye makolo ndi abale awo mumdima pozindikira kuti ubale wawo sudali wachibwana. +Titakambirana, tidadziwitsa abale ndi makolo kuti azidziwa chifukwa timazindikira kuti pokangopita nthawi pangono tiwafuna kuti atimangire chinkhoswe ndi kutigwira dzanja pomwe tikukalowa mbanja, adatero Dennis. +Iye akuti adakhala choncho mpaka chaka cha 2014 pa 9 August pomwe adamanga chinkhoswe nkuyamba kukonzekera ukwati omwe udachitika pa 2 April ku tchalitchi cha Katolika cha Maula ndipo madyerero adali ku Peak Gardens mumzinda wa Lilongwe. +Sheila ndi mkazi wanzeru, wokongola, wachilungamo, wodzisamala ndi woopa Mulungu. Adandiwonetsa chikondi chenicheni monga momwe makolo anga adandionetsera, adatero Dennis. +Dennis ndi mwamuna wolimbikira, wodzichepetsa ndi wachikondi komanso wachilungamo. +Amandilimbikitsa ndikakhala ndi chofooka ndipo amandiphunzitsa kuthana ndi zokhoma, adatero Sheila. +Anatchezera Nditani Anatchereza? Agogo, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndine mtsikana wa zaka 20 ndipo ndili ku koleji. Ndili ndi chibwenzi chomwe tidagwirizana kuti tidzamange banja mtsogolo muno. Mnzangayu amati akufuna kuti adzandidziwire mbanja chifukwa akayamba kundigona panopa atha nane filimu. Ndiye akuti poti iyeyu ndi munthu pena zimavuta ndiye akuti akufuna apeze mkazi woti azigonana naye popewa kugonana ndi ine kuti inyeyo adzandikwatire. Kodi kumeneku ndi kukonda? Ndithandizeni, agogo, nditani. +Ndi L, Likuni, Lilongwe Wokondeka L, Funso lako ndalimva ndipo ndikuti wafunsa bwino zedi. Bwenzi lakolo ndi munthu wachilungamo, koma chilungamo chake chaonjeza. Munthu wotere osamukhulupirira chifukwa ndi kamberembere. Iyeyu wanena chinthu chanzeru kwambiri kuti pakalipano musamagonane chofukwa akuopa kuti akatero atha nawe chilakolako chifukwa wakudziwa. Koma akuti akufuna apeze mkazi wina wapambali kuti azikapumirako poti iye ndi munthu, nanga iwe wakuuza kuti nawe utha kupeza wina woti uzicheza naye pamene mukudikira kuti mudzakwatirane? Akunama ameneyo; akufuna kuti azioneka ngati munthu wokhulupirika pomwe ndi wachimasomaso ndi akazi ena. Tikamati kudzisunga ndi nonse awiri, osati wina aziti mnzangawe udzisunge koma ine ndikayendayenda. Kunjaku kwaopsatu, ndiye wina azipanga dala zachibwana ngati zimene akunenazo, si zoona ayi. Ngati ndi wachilungamo, iyenso ayenera kupirira kuchilakolako cha thupi kufikira tsiku lomwe mudzalowe mbanja. Koma ngati adayamba kale zogonana ndi akazi ena, mchitidwe umenewo sadzausiya. Ndiye, kunena zoona, mwamunayo sali woyenerera kumanga naye banja chifukwa alibe chikondi chenicheni ndi iwe. Amati mbuzi ikalawa mchere sigwirika! Amandikakamiza Agogo, Ndine mtsikana wa zaka 16 ndipo ndili ndi bwenzi langa wa zaka 19. Iyeyu amandikakamiza kugonana naye. Ine zimenezo sindimafuna koma ndimalola kupanga naye zimenezo chifukwa ndimamukonda kwambiri ndipo kukana ndimaopa kumukhumudwitsa. Ndiyeno ndipange chiyani kuti mchitidwewu uthe? Zikomo. +Tidakumana Bwanji: Padali pagalaja ku Area 25 Garage ndi malo okonzera galimoto, koma ukachita mphumi malowa uthanso kudya nawo bwino monga momwe Mike Tembo adachitira. +Iyetu adasodzerapo msoti womwe akumanga nawo banja pa 7 May pa Sana Multi-Purpose Hall mumzinda wa Lilongwe. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mike Tembo amagwira ntchito ku Leyland Motors koma amadziwika kwambiri chifukwa cha udindo womwe adali nawo kutimu ya Silver Strikers komwe ankagwira ngati mlembi. Njole yomwe mkuluyu watola ndi Annie Nkhandwe yomwe ikugwira ntchito ku JTI. +Annie ndi Mike patsiku la send-off Mike akuti mudali mu December 2013 pamene Mulungu adayamba kulumikizitsa awiriwa. Iye akuti adapita kugalaja ya ku Area 25 komwe amakakonzetsa galimoto. Amadikira kuti mpaka aikonze. +Akutitu mpaka cha mma 6 koloko madzulo ali pomwepo, anthu atayamba kuweruka ndipo apa naye Annie ataweruka amadutsira mbali yomwe kudali Mike. Apa nkuti awiriwa asakudziwana. +Koma likalemba lalemba basi, Mike adanunkhiza mafungo ndipo adamulonda mtsikanayo ngakhale samamudziwa. Moni ndi amene adali woyamba ndipo adasiyana atangofunsana maina. +Mosachedwa galimotoyo akuti adamaliza kukonza koma Annie nkuti atanyamuka kale. +Sindidachedwe, koma kukailiza kuyamba kumulonda mpaka ndidamuona akulowa pageti yakwawo. Ndidamukuwira, iyeamvekere, you were following me? Apo ndidalankhula molimba mtima ndimvekere, ndimafuna ndidzaone pamene my future wife akukhala ndipo adaseka, ine ulendo, adamusereula motero. +Kuchoka apa, awiriwa akuti amakumanabe, koma Mike akuti adapanga kaulendo kokaonera mpira wa Zambia pa Taytaz mmbali mwa msewu wa Mchinji osadziwa kuti mkuluyu alindi zina zoti achite kupatula mpirawo. +Chichewa chidagwa, namwali adayesera kuzemba koma Mike sadasinthe mawu. Njoleyi akuti idangomuuza kuti ukhale kaye serious. Mike adaonetsa izi ndipo ubwenzi udayamba. +Awiriwa apanga kale send-off sabata yatha pamene akukonzekera ukwati. +Mike amachokera mmudzi mwa Kamuthuleni Tembo kwa Inkosi Mtwalo mboma la Mzimba pomwe Annie ndi wa mmudzi mwa Kamunthambani Nkhandwe kwa Mtwalo komweko ndipo onse akuchokera kumabanja achifumu. +Lidali tsiku la Big Sunday Sangwani Mwafulirwa tsopano ndi bambo, si mnyamatanso monga ena akumudziwira chifukwa dzulo pa 4 June 2016 wamulonjeza Trufena Chiwaya, mwana wa mmudzi mwa Muleso kwa Senior Chief Somba mboma la Blantyre kuti sadzamusiya mpaka imfa. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Sangwani ndi mneneri wa bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission pamene Trufena akugwira ku Western University of Malawi. +Kukwaya ya mpingo wa Living Waters ku Ndirande ndiko kudayambira kukumana kwa awiriwa. Sangwani, yemwe kwawo ndi ku Ndirande mumzinda wa Blantyre, akuti panthawiyo iye adalibe khumbo lothira Chichewa namwaliyu. +Amangondisangalatsa khalidwe lake. Zachibwana ayi, zibwenzi ayi, nthawi zonse chidwi ndi Mulungu wake. Izi zidandipatsa chidwi, adatero mneneriyu. +Sangwani ndi Trufena pano ndi thupi limodzi Ndimadziwa kuti makolo anga akwiya akamva zoti ndapanga chibwenzi, komanso ndimafuna ndikafike ku University, adaonjeza Sangwani. +Nthawi idakwana kuti awiriwa asiye kucheza zamapemphero zokhazokha. Ngakhale Sangwani adalibe maganizo, komabe Mulungu adazikonza. +Zonse zidayambika pamene mayi ake a Trufena adamwalira ku Ndirande, zomwe zidachititsa namwaliyu kuti abwerere kwawo kwa che Somba. Kuiwalana ndi Sangwani kudali komweko. +Patatha masiku ndidayamba kumukumbukira. Kodi moyo wake uli bwanji? Kodi akulimbikirabe kupemphera? Khumbo lomuyendera lidalipo koma padalibe amene amadziwa komwe ankakhala, adatero Sangwani. +Koma tsiku lidakwana kuti akumanenso. Uku tsopano kudali ku Big Sunday yomwe idachitikira ku Living Waters Church ku Chimwankhunda mumzinda wa Blantyre. Kumeneko ndiye kudali kufunsana zambiri ndipo Sangwani adadziwa komwe namwaliyu akukhala. +Pakutha pa masiku angapo, Sangwani adakwawira kwa che Somba. Mofunsira njira, iye adakwanitsa kukakumana ndi namwaliyu. Apo padali pa 8 July 2001. +Ndinenetse kuti ndinalibe maganizo ofunsira koma kukangomuona. Tikucheza, nkhani zidandithera, kenaka ndidatulutsa mawu achikondi, adatero Sangwani. +Naye Trufena adati: Ndinadabwa akundiuza zachibwenzi. Ndinali ndisanapangepo chibwenzi, padalibenso zoganiza koma kumuyankha pomwepo kuti zimenezo sindimapanga. Adandikakamira ndipo ine ndinayamba kudabwa naye. Kenako maganizo adandifikira kuti ngati munthuyu wayenda mtunda wautali ndiye kuti watsimikiza. Moyo wanga udavomera, ndidamulola. +Phyzix wadza ndi Captain Long John Patapita zaka zingapo akutchuka ndi nyimbo zomwe zidavuta monga Cholapitsa, Gamba, Chilombo, Abwana, Memba, Town Monger, Man phyzo, Handsome, The Leasder ndi Gamba wa Suit, Noel Chikoleka, yemwe amadziwika kuti Phyzix pankhani zoimba, wadzanso ndi chimbale china chotchedwa Captain Long John. Monga mwachizolowezi nyimbo za mkuluyu zimakhala ndi chikoka. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye zokhudza chimbale chatsopanochi motere: Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndikumbutsane dzina lija Phyzix: Muyembekezere chimbale cha nyimbo zothyakuka Dzina langa ndi Noel Limbani Jack Chikoleka, ndimachokera mmudzi mwa Mwamadi, T/A Kambwiri mboma la Salima. Dzina lodyera ndine Phyzix. +Ulipa uli ndi zimbale zingati za nyimbo? Chiyambireni kuimba ine ndatulutsapo zimbale 5 koma zitatuzo ndimangotulutsira pamakina a internet ofuna amagulira pamenepo nyimbo zanga. Chimbale chomwe ndidatulutsa nkumwaza pamsika chidali chomwe ndidatulutsa mchaka cha 2005 chomwe chidali ndi nyimbo ya Cholapitsa. Nthawi imeneyo ndili ku Mzuzu University. +Pano ukumveka kuti ukutulutsa chimbale china, chimenechi ndi chimbale chanji? Chimenechi ndi chimbale chomwe ndikuchitcha Captain Long John ndipo chili ndi nyimbo 10. Nyimbo 6 zatuluka kale ndipo zina zotsalazo zituluka nthawi ina iliyonse kuti anthu asangalale ndi nyimbo zina zophikidwa bwino. +Chimbale chimenechi chituluka motani? Chimbale chimenechi chituluka mwaluso lapadera. Poyamba, nyimbo zonse zizituluka ngati ma singles (imodziimodzi) ndipo zonse zikhala ndi wowonerera zomwe. zonse zikadzatha ndidzakhazikitsa chimbale kuti anthu azidzatha kukhala nacho ndi kumvera kuyambira nyimbo yoyamba mpaka yomaliza chifukwa ndikudziwa kuti akangomva imodzi pawayilesi kapena kuona pakanema azikhala ndi njala yaikulu yoti amvereso inzake pokhapokha chimbale chonse chidzathe mpomwe anthu adzakhale ndi mwayi wotere. +Uthenga munyimbo za mchimbalechi ndi wotani? Muli uthenga osiyanasiyana, monga munyimbo ya Ndekha muli uthenga wa chisangalalo cha ukwati. Ndidaipeka makamaka polemekeza ukwati wanga koma ndidaimba moti anthu enaso akhoza kuigwiritsa ntchito polemekeza ukwati wawo. Mfana Wolusa ndi munthu wachangu patauni osafuna kulekerera kanthu ndipo ndi nyimbo yokoma kwambiri. Baby OldSkool ndi nyimbo yomwe imakamba za mkazi wotsogola, odziwa zambiri zakale ndi zatsopano. Mkaziyu ali ndi chikoka koma amachititsa mantha kumufikira ndiye mkatimo ine ndikuyesa kumufikira. One Meets Two imatanthauza kukumana kwa ine ndi akadaulo anzanga Marcus ndi GD, omwe akhala akundithandiza munyimbo zambiri ndipo ndikupitirira kwa nyimbo ya Lone Ranger. Kwa omwe amatsatira Lone Ranger akhoza kukhala ndi chithunzithunzi cha nyimbo yatsopanoyi. Nyimbo zinazo sizidatuluke koma nazoso zili ndi uthenga wapamwamba kwambiri moti anthu adzazikonda zikatuluka. +Tangotiuza momwe udabwerera muzoimbazi? Nthawi yomwe ine ndimayamba kuimba, oimba chamba cha Rap tidalipo ochepa kwambiri ndipo nyimbo ikatuluka imakhala nthawi yaitali isadalowe pansi. Pangonopangono ena adayamba kubweramo koma panthawiyo kudali kovuta kupeza mwayi wa makina a internet zomwe zinkatipangitsa enafe kuti tizisowa njira zopititsira patsogolo luso lanthu. +Mpando Wamkulu afika pa Wenela Abale anzanga, tsikulo kudali nyimbo zija zogawa tonse pa Wenela. Adayamba ndi Patience Namadingo, yemwe waimba Nyimbo yotamanda uja mneneri wathu Majuscule Profit Bashiri. Musandifunse kuti dzina ili lidabwera bwanji chifukwa sindikuuzani. Ndipo mukadziwa mukufuna muchitenji? Sinjenjemera ndiyo nyimbo adayamba kuika Gervazzio. Iyitu ndi nyimbo imene ikutamanda kuti Majuscule Profit Bashiri akunenedwa kuti ngakhale alasidwe mikondo yamoto, sanjenjemera. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Wina uyu. +Idaikidwanso nyimbo ya anyamata ena, ati kuyankha ija ya David ya Osaopa. Sindikudziwa kuti nyimbo ya anyamatawa kwenikweni akumati chiyani, koma akumanenamo zakuti iwo sakuopa. Kaya sakuopa chiyani? Pasanathe nthawi idaikidwanso ya Kalawe, yotamandira Bashiri. Adaikanso nyimbo ija ya Onesimus (ndikumva kuti uyu ndi mbale wake wa Twosimus!). Iyetu ndiye adabwera ndi nkhani ati Miracle Money. +Major do it! I need money In my pocket In my wallet In my handbag In my bank account. +Koma isanathe, kudabwera nyimbo ya Osaopa, ya David. +Muli ulaliki umo! Ndapha mikango, akutero. Sindilekerera ngati mikango ipha ziweto zanga! Sindichita mantha ngakhale kulekerera ngati nkhosa zanga zijiwa ndi mikango. Ndaphapo mikango ngakhalenso zimbalangondo ndiye sindingaope Mfilisiti wosaumbala akuzunza anthu anga. +Komatu izi za miracle money ndizo zikuchititsa ambiri kukhala aulesi. Nanga taonani a mipira akuti koma miracle money! A nkhonya nawonso akuti miracle money, adatero Abiti Patuma. +Tidangozindikira Majuscule Profit Bashiri watulukira, amvekere: Ndili pano ndi miracle money! Ndani akufuna chozizwa? Kukonda ndalama ndicho chiyambi cha uchimo. Ngati aneneri odzodzedwa akuyamba kuzika mzimu wokonda ndalama mwa nkhosa zawo, zitha bwanji? Zanuzo ife ayi. Sitifuna kupempha ndalama monga achitira ena. Ife kwa inu tipempha pemphero kuti Mulungu atipatse nzeru zopezera ndalama. Komanso sitingapemphe kwa Mulungu kudzera mwa inu chifukwa simunakhalepo Yesu, adatero Abiti Patuma. +Mawu ake ali mkamwa adatulukira Mpando Wamkulu. +Mumadziwa inu za kuchitekete? Mumawadziwa inu anyamata a patauni? Mumamvetsa za changu pamalo? Lero ndabwera. Mwana uja amafuna kundipinga wazitaya. Si nkhanitu ya miracle money iyiyi, ayi, adatero iye. +Abale anzanga, munthu uyu sindimumvetsa. Sindidzamumvetsa. +Mwayenera. Ifetu titangomva kuti ena akukomoka tidadziwiratu kuti zavuta, adatero Abiti Patuma. +Palibe ndidatolapo. +Izi ndikuchita chifukwa ndidasolola zochepa kuposa Adona Hilida ngakhalenso Mfumu Mose. Nkadadziwa kuti ndalamazi nzophweka chonchi, mukadamva zina. Ine ndi nyatwa, adatero iye. +Zidandipitanso. +Palibe angamange mvula, siyani kuzunza anthu Masiku apitawa anthu 7 adawagwira ku Chiradzulu ndipo adawazunza powaganizira kuti akumanga mvula. Adawakolezera moto masanasana kuti aothe ndipo akuti anthuwo atangonena kuti mvula ibwera, adawasiya ndipo mvula ikulikitika mpaka lero. Kodi munthu angathe kumanga mvula? Nanga amamangira chiyani? BOBBY KABANGO akufunsa mneneri wa zanyengo Elina Kululanga kuti afotokoze zomwe zimachitika kuti mvula igwe kapena isagwe madera ena motere: RAINING Pali zikhulupiriro zoti mvula ikamavuta, monga yavutira chaka chino maka madera a chigawo chakummwera, ndiye kuti ena akuimanga dala. Inu monga a zanyengo mukuti bwanji? Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ayi, ndipo sizingatheke munthu kumanga kapena kugwetsa mvula. +Nanga mvula ikuvuta chonchi bwanji? Iyi tsopano ndi nkhani ya kusintha kwa nyengo. Mpweya woipa womwe tikulandira ndiwo ukuchititsa kuti mvula ikhale yovuta chonchi. Nkhani iyi ndi ya dziko lonse komanso maiko ena akukumananso ndi vutoli, si kuno ku Malawi kokha, ayi. +Kodi zatani kuti chaka chino tikumane ndi mavutowa? Nkhani ndi kusintha kwa nyengo. Kuti mumvetse chomwe chikumachitika ndi ichi: mitambo ikumakungana bwinobwino kusonyeza kuti mvula ibwera. Mphepo yoipa ikangowomba, basi mvula singabwerenso ngakhale mitambo itachuluka maka. +Kodi kale lonse mphepo imeneyi idali kuti? Mumvetsetu, ndati kusintha kwa nyengo, kalelo chilengedwe chidali chonse, koma pano chilengedwe chasokonekera. +Ndiye mukukana kuti wina sakumanga? Osatheka, ndipo padziko lapansi palibe ngakhale singanga kapena mfiti yodziwa motani amene angamange mvula. +Anthu amene adawagwira ku Chiradzulu adauza gulu kuti mvula igwa mawa lake ndipo zidatheka, ndiye mwati awawa mvula sadaimange? Inuyo mumamvera za nyengo? Chifukwa sabata yatha takhala tikulengeza kuti sabata ino yonse mvula igwa kwambiri kuchigawo cha kummwera, ndiye mukudabwanso pamene mwaona mvula ikubwera? Bwanji mvula ikumabwera mudzi umodzi wina osabwera poti ndi pafupi? Izi ndiye zomwe zikutsimikiza kuti nyengodi yasintha, apopo ndiye kuti pakukutanthauzirani kuti mphepo yoipayo idakhudza mbali ina kwina ayi. +Inuyotu mwakhalapo kumudzi, monga kalelo simumakhulupirira kuti anthu amamanga mvula? Ndinkakhulupirira, koma nditabwera kunthambi ya zanyengo ndi kuona momwe zimakhalira kuti mvula igwe, ndidadziwa kuti ndinkadzinamiza. +Ndiye kuti inuyo azanyengo mumamanga mvula, eti? Ayinso, ifeyo timangoona momwe mphepo ikuyendera ndipo kuti kuyenda kwake kukutanthauza chiyani. Tikaona ndi pamene timalengeza momwe mvula ibwerere komanso momwe kutenthere ndi kuzizira komwe. +Mutani kuti anthuwa akhulupirire kuti munthu sangamange mvula? Azimvera wailesi momwe zanyengo zikuyendera komanso azitifunsa. Tikhalanso ndi nthawi yowaphunzitsa anthu za nyengo mwezi umenewu. +Ngati wina akuti amatha kumanga mvula, mumutani? Ndatitu palibe amene angathe, koma ngati ena akutero ndiye abwere kuno adzatitsimikizire. +Nanga mphenzi yokha ndiye munthu angapange? Ayinso, izo ndi bodza. Palibe angapange mphenzi ndipo sadzapezekapo. Zonse ndi zokhudza chilengedwe. +Obindikira mnyumba azengedwa mlandu Bwalo la milandu la majisitireti mumzinda wa Blantyre lakhazikitsa Lachitatu, 25 May, ngati tsiku lomwe lidzapereke chigamulo kwa banja lina lomwe lakhala likudzitsekera mnyumba kwa zaka zitatu ndi kulephera kupereka chisamaliro kwa ana awo anayi. +Govt to review Genset deal MBC clean up APM aide nabbed Mneneri wa nthambi ya zachilungamo, Mlenga Mvula watsimikizira Msangulutso za nkhaniyi. +Mvula adati nkhaniyi idalowa mkhoti pa 13 May ndipo banjali lidakana mlandu wolephera kupereka chithandizo kwa ana awo ndipo ilowanso mbwaloli Lachitatu likubwerali pa 25 May pamene oimira boma abweretse mboni. +Adakana kulakwa: Banda ndi mkazi wake akuyankha mlandu wosapereka chisamaliro kwa ana awo Sabata yatha, apolisi ya Manase mumzinda wa Blantyre adanjata Peterson Mtchini Banda, wa zaka 44, ndi mkazi wake Agnes, wa zaka 41, atatsinidwa khuku kuti banjali silimatuluka mnyumba kuyambira mchaka cha 2013. +Mneneri wa polisi ya Blantyre, Elizabeth Divala, wauza Msangulutso kuti banjali lidauza apolisiwo kuti adachita izi ngati njira imodzi yodzitetezera kwa anthu achipongwe. +Akuti tsiku lina bamboyo adafuna kuchitidwa chipongwe ndi anthu ndipo nkhaniyo ati adafotokozera apolisi koma sadaione mutu wake. Kuyambira panthawiyo, iye akuti adauza banja lake kuti asadzatulukenso mnyumbamo, adatero Divala. +Moti tsiku lomwe tidapita kunyumbako, tidagogoda koma sadatsegule, tidagwiritsira ntchito mphamvu pothyola chitseko ndipo tidawapeza makolowo komanso ana awo anayi akuoneka ofooka. Tidawatengera kupolisi kuti tidzawafunse. +Banjali akuti lidauza apolisiwo kuti akafuna ndiwo, kapena chakudya chilichonse, amaitana anthu amene ayandikana nawo ndi kuwapatsira ndalama kuti akawagulire zomwe akufunazo. +Nyumbayo ili kumpanda, ndiye chilichonse chili kumpandako monga chimbudzi komanso madzi. Ali ndi nyumba za lendi zomwe amatolera ndalama pakutha pa mwezi, ndalama amazipeza motero ndipo ati amadzawapatsira ndalamazo pazenera, adatero Divala. +Chidzitsekerereni mnyumbamo mu 2013, ana a banjali akuti adawaleketsa sukulu. Pano mwana woyamba ndi wa zaka 17, wina 14, wina 11 ndi wina wa zaka zinayi. +Divala wati makolowo adawatsegulira mlandu wolephera kupereka chithandizo kwa ana awo. +Anatchezera Sakufuna kukayezetsa Anatchereza, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndakhala ndili pachibwenzi ndi mtsikana wina kwa chaka chimodzi ndipo timakondana kwambiri. Ndine Mkhristu ndipo ndikhulupirira kuti sibwino kumagonana ndi wachikondi wako musadalowe mbanja lomanga. Ndakhala ndikumva malangizo oti masiku ano ndi bwino kukayezetsa magazi musanaganize zolowana, koma mnzangayu nditamuuza zimenezi adati ine zimenezo ndiye ayi. Kumufunsa chifukwa chake adati ineyo ngati ndikudzikaikira ndipite ndikayezetse, osati iyeyo. Akuopa chiyani? MCJ Lilongwe Zikomo MCJ, Mwafunsa bwino! Akuopa chiyani ameneyo? Pali bii, pali munga, ife akale timatero. Chilipo chimene akuopa chifukwa akanakhala kuti ali bwinobwino, si bwenzi akuchita kukanira patalitali kuti ine toto, pita wekha. Kudziwa mmene munthu ulili usanalowe mbanja ndi chinthu chabwino kwambiri, makamaka masiku ano pamene kuli mliri wa kachilombo ka HIV/Aids. Mundimvetse bwinobwino pamenpa: si kuti munthu akapezeka ndi HIV ndiye kuti sayenera kukwatira kapena kukwatiwa, ayi. Munthu aliyense ali ndi ufulu wokhala pabanja, koma zimakhala bwino kudziwa mmene mthupi mwako mulili pofuna kukonza tsogolo la banja lanu. Ngati wina apezeka ndi kachilombo kapna matenda ena alionse mumadziwa chochita pofuna kudziteteza kuti nonse mukhale moyo wathanzi. Komanso ngati mukufuna mwana mbanja mwanu madotolo amadziwa njira zokuthandizirani kuti mwana wanu asatenge nawo kachilomboko. Chachikulu ndi chikondi pakati panu-pali chikondi palobe mantha. Mufotokozereni wokondedwa wanuyo zimenezi kuti amvetsetse, koma ngati akumenyetsa nkhwangwa pamwala, musiyeni ameneyo, muyangane wina amene angakumvetsetseni pankhani yoyezetsa magazi. +Nsalu ya lekaleka Anatchereza, Ine ndi mwamuna wanga takhala pabanja zaka ziwiri ndipo nthawi yonseyi takhala tikugwiritsa ntchito njira zolera chifukwa mwamuna wanga amati nthawi yoti tikhale ndi mwana sinakwane-titoleretolere kaye kuti tisadzavutike tikadzakhala ndi mphatso ya mwana mnyumba mwathu. Kunena zoona zimene amati titoleretolere kaye sindikuziona, komanso anthu kunjaku ndiye akumatiseka ndi kumatinyogodola kuti sitibereka, ati mwina amunanga adakakhomera ku Dowa. Ine ndiye ndatopa nazo zimenezi. +Anatchezera Sakundilipira Zikomo gogo, Ndakhala ndikugwira ntchito kukampani ya alonda ina kwa miyezi 11 popanda masiku opuma. Mwezi ulionse amatidula K500 ati ya yunifolomu. Ndidasiya ntchito mwezi wa December chifukwa amachedwa kulipira. Pakatha miyezi iwiri amatipatsa za mwezi umodzi. Ndalama za mwezi wa December mpaka lero sanandipatse. +HP, Zomba. +HP, Kampani imeneyo ndithu mukhoza kuitengera kukhoti la makampani. Poyamba amakuberani kukulipiritsani yunifolomu. Izi ndikunena chifukwa yunifolomuyo imakhala ya kuntchito osati yanu. Idali ngati chimodzi mwa zipangizo zanu za ntchito. Kodi angakuduleni malipiro chifukwa mukugwiritsa ntchito chibonga cha kampani? Mukhozanso kukadandaula kuofesi ya zantchito mboma lanu ndipo akakuthandizani. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Zonse ndine Gogo wanga, Ndimagwira ntchito ya mnyumba koma chilichonse pakhomo ndimachita ndine kuyambira kusamala mnyumba, kuphika, kusesa panja, kusamala mwana kutsegula pageti, kuchapa ndipo zonse ndimagwira mwana ali kumsana olo akhalepo makolo a mwana sakundilandira mwana wawoyo. Ndithandizeni, Anatchereza, nditani pamenepa? TM, Mulanje Zikomo TM, Inuyo pamene munkafunsira ntchito kwa bwana wanu mudafunsira ntchito yanji? Ndafunsa choncho chifukwa nthawi zonse munthu ukamafunsira ntchito bwana amakufunsa kuti ukufuna ntchito yanji? Tsono ngati pali ntchito yoonjezera mumachita kugwirizana malipiro ake. Koma mmene mwayalira nkhani yanu zikuoneka kuti abwana anu ngovuta ndipo alibe chikondi. Kagwiridwe ka ntchito motere ndi ukapolo. Makamaka zandimvetsa chisoni kumva kuti chilichonse mumagwira nokha mwana ali kumsana ngakhale makolo ake alipo. Uku ndiye nkusowa chikondi ngakhale kwa mwana wawo yemwe. Tsono ngati chili chizungu kuti chilichonse azisiyira watchito, tsiku lina adona mnyumbamo adzasimba tsoka. Ndaonapo ine abambo ena akukwatira mtsikana wantchito kusiya mkazi wawo ati wantchito akukwaniritsa chilichonse mnyumbamo. Amayi otere, omwe amasiyira wantchito chilichonse pakhomo iwo ali tambalale kumapenta milomo ndi zikhadaba pamkeka kapena pasofa, asadandaule zikawachitikira zotere. Amuna ambiri amalakalaka atadyako zophika akazi awo, koma haa, zonse amvekere wantchito aphika! Basopo! Samalani nazo zimenezo. Tsono inu a TM, musadandaule kwenikweni kuti ntchito ikukuchulukirani, pitirizani kugwira modzipereka, simudziwa chomwe Mulungu wakukonzerani. Tsiku lina mudzalandira mphotho yanu chifukwa cha kulimbikira ntchito pakhomo. Ndemanga Anatchereza, Ndati ndiikirepo ndemanga pankhani yomwe munalemba chaka chatha ya mzimayi yemwe akuti mwamuna wake amamubisira kuti amamwa ma ARV. Mayiwa athokoze Mulungu kwambiri pakuti apulumuka ku likukumwe la matenda ndipo asachedwenso, apite kukhoti kukamangala. Mwamunayo ndo woopsa kwambiri akufunika chilango chachulu Ine Mzungumbuli, Lilongwe. +Anatchezera Anzanga sakundifunsira Ndine mtsikana wa zaka 20, vuto ndili nalo ndi loti sindikufunsiridwa ndi anyamata amsinkhu wanga koma okwatira okhaokha. Kodi agogo nditani pamenepa? Kapena ndingosiya kulola anthuwa ndi kumangokhala single? Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu EDS, Lilongwe Zikomo EDS, Kuti uzifunsiridwa ndi anthu amene ali kale pabanja vuto lako ndi chiyani? Funsoli udzifunse wekha ndipo yankho ulipeza. Kodi umakonda kucheza ndi anthu otani-achinyamata anzako kapena akuluakulu oti si amsinkhu wako? Chifukwatu ngati umacheza ndi achinyamata anzako sipangalephere wina kukhala nawe ndi chidwi. Chimodzimodzi ngati umakonda kucheza ndi amuna oti ndi okwatira iwe nkumawagonekera khosi, chowalepheretsa kukufunsira nchiyani? Mwina anyamata sakukufunsira chifukwa akudziwa mbiri yako yoti umakonda ma sugar daddy. Ndiye madzi asanachite katondo, usiye kuwalola ndipo uyambe kucheza ndi achinyamata anzako. Mwana mngonongonowe chofuna kupasulira mabanja a eni nchiyani? Tachokera kutali Ndine mtsikana wa zaka 20 ndipo ndakhala pachibwenzi ndi mnyamata wina kwa zaka 4. Poyamba pa chibwenzi chathu timakondana kwambiri koma panopa zinthu zinasintha ndipo ndikuganiza kuti mwina adapeza chibwenzi china ngakhale amakana ndikamamufunsa. Izi zili choncho ndimakanika kuti ndikhalenso pachibwenzi ndi munthu wina chifukwa ndimaganiza kaye komwe tachokera. Nditani naye mnyamata ameneyu, ndikhale nayebe kapena ndingosiyana naye? Chonde ndithandizeni. +LK, Ntcheu Mwana wanga LK, Amati fupa lokakamiza silichedwa kuswa mphika. Chikondi sakakamiza. Monga wanena, udayamba kukhala ndi chibwenzi uli ndi zaka 16, cholinga cha chibwenzi chanucho chidali chiyani? Mumafuna kudzakwatirana pambuyo pake kapena adali masanje chabe? Mmene ndikuonera chidali chibwana ndipo pano mnzakoyo watha nawe chidwi, ndipo sakukufunanso. Ndiye madzi asadafike mkhosi musiye, uone zina. Udakali mwana wamngono, moti utaika mtima pasukulu sulakwitsa ayi. Ameneyo asakutayitse nthawi, ganiza za tsogolo lako. +Njala ikhaulitsa a Malawi Ma Admarc ena kuli gwagwagwa! Zafika pena. Ngati wina samwalira ndi njala ungokhala mwayi chabe koma zinthu zaipa mdziko muno moti anthu ena akugona kumimba kuli pululu. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika akunenetsa kuti palibe amene amwalire ndi njala, koma ngati sipachitika china chake mmisika ya Admarc mdziko muno ena amwalira nayo. +Mzere wa ofuna kugula chimanga ku Admarc Ulendo wa Tamvani mmaboma a chigawo cha kummwera, pakati komanso kumpoto, wapeza kuti madera ena patha miyezi ingapo chimanga chikusowa mmisika ya Admarc. +Ma Admarc a Chikomwe, Ngwerero, Nasawa, Mayaka, Sunuzi, Jenala, Zaone ndi Buleya mboma la Zomba kwa T/A Mbiza akuti atha miyezi iwiri kulibe chimanga. +Gulupu Belo wati malinga ndi kusowa kwa chimangacho, anthu amagonera deya amene amagula pamtengo wa K240 pa kilogalamu. +Panopa amene wapeza gaga ndi munthu. Chakudya chasowa, moti ndatumiza anthu 8 kuchipatala amene amaonetsa zizindikiro zachilendo chifukwa chosadya, adatero Belo. +Ku Mwanza malinga ndi T/A Kanduku, miyezi iwiri yatha chimanga kulibe. Iye wati poyamba anthu amagonera mango koma lero ndiye kolowera kwasowa. +Ndi nkhani yosabisa, njala yavuta kuno ndipo chimanga chatenga nthawi chisadafike ku Admarc, adatero Kanduku. +Ku Balaka patha miyezi iwiri chimanga chisadafike pa Admarc ya Phalula pamene kwa Sosola ndiye patha mwezi. +Sabata yatha tidapeza anthu ammudzimo akupita kukadandaula kwa DC wa bomalo chifukwa akhala akuuzidwa kuti chimanga chibwera koma kuli chuuu. +Admarc ya Misuku ku Chitipa ikumalandira chimanga mwezi ulionse kamodzi koma chimangacho chikuchokera kubungwe la World Vision. Admarc ya Chikwera mbomalo ilibiletu chimanga, pamene Admarc ya paboma yangolandira kumene matumba 300. Mabanja 2 000 ndiwo amadalira Admarc ya pabomayo koma ikugulitsa makilogalamu osaposa 15 kwa aliyense. +Admarc ya pa Karonga boma ili ndi chimanga koma pamene timafikapo Lachiwiri msabatayi nkuti pali mnzere wotalika ndi mamita 280. Anthu akumagona pomwepo kuti agule chimanga. +Ma Admarc a boma la Nkhata Bay akuti akumalandira chimanga pafupipafupi koma chikumatha tsiku lomwelo chifukwa chikumafika chochepa kuyerekeza ndi anthu amene akufuna chakudyacho. +Mkulu wa bungwe la Admarc Foster Mulumbe wati chiyambireni September chaka chatha agulitsa matani 26 000 a chimanga. Iye watinso kufika pano, Admarc yatsala ndi matani ochepa. +Chimanga chidakalipo koma chochepera, ndipo tikupitiriza kupereka mmisika yathu. Ngati chimanga chatha mmisika yathu, ndi bwino kutidziwitsa msanga kuti titumize china, adatero Mulumbe. +Miyezi ingapo yapitayo, boma lidagula matani 30 000 a chimanga mdziko la Zambia. +Woyendetsa ntchito wamkulu mu unduna wa malimidwe Bright Kumwembe wati chimanga chonsecho chidapita kumisika ya Admarc. +Chimanga chonsecho chidafika mdziko muno ndipo chili mmisika ya Admarc. Likulu losamala chakudya la National Food Reserve Ageency [NFRA] likugula chimanga china mdziko momwe muno, adetro Kumwembe. +Nkhani ya njala si yachilendonso mdziko muno. Bungwe la World Food Programme (WFP) lati lakwanitsa kufikira anthu 1.6 miliyoni mmaboma 15 amene ali pamoto wa njala. +WFP Lolemba lidatulutsanso lipoti lina lomwe limati anthu 14 miliyoni ali pachiopsezo chokukutika ndi njala kummawa kwa Africa. +Dziko la Malawi ndi limodzi mwa maiko okhudzidwa chifukwa cha mavuto a kusowa kwa mvula. +Chisamakome mbuzi kugunda galu Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kawirikawiri tikamva za nkhanza zozungulira chuma cha masiye, timaganizira kuvutidwa kwa amayi ndi ana mmanja mwa abale a mwamuna yemwe wamwalira. +Ichi nchifukwa chakuti nthawi zambiri, mzimayi osiyidwa ndi ana ndi omwe amalandidwa katundu nkumasowa mtengo ogwira akakhala kuti amadalira bambo wopitayo pachilichonse. +Koma polunjika maso pa amayi ndi ana, timaiwala ena mwa anthu amene nthawi zina saganiziridwa pankhani yogawa chuma cha masiyemakolo komanso abale amalemu. +Chimakhumudwitsa kwambiri nchakuti amayi ena amasiye, akakumana ndi abale a mwamuna aulemu, amakhala patsogolo kuphangira zonse kuti zikhale zawo ndi ana, kuponya miyala anthu omwe adachita chilichonse chotheka kuti mwamuna wawo aleredwe bwino. +Osamaiwala kuti ngakhale mwamuna mwaberekerana naye ana, ngakhalenso kupezera chuma china limodzi, mbali ina yamaziko ake ndi makolo ndi abale amene adamulera, nkumuongolera kufikira kukula kuti inu muthe kumukonda. +Mmene inu mumawerengera kuti pali munthu womudalira, momwemonso makolo ndi abale ena amadalira pomwepo. +Inde chuma chamasiye chambiri chiyenera kupita kwa ana, omwe amayenera kuti aphunzire, koma izi sizitanthauza kuti ena omwe amadalira malemuyo aiwalidwe. +Mumati iwowo alowera kuti? Odalira malemuwatu sakutanthauza omwe amawerengera ndalama zamalemuyo pa chakumwa, ayi. Sindikukambanso za abale ena achibwana osafuna kugwira ntchito nkudziimira paokha. +Ndikukamba za makolo okalamba; anthu ngati abale angonoangono omwe chifukwa cha umasiye amadalira mchimwene wawo. +Kanthu nkhama: Alimi akuchita kuthirira fodya Kudula kwa mvula kutionetsa zachilendo mpaka alimi kuchita kuthirira mminda ya fodya kuti mwina angaphulepo kena kake. Alimi ochenjera akuyesetsa kupulumutsa mbewu zawo pothirira ngakhale kuti ntchitoyi ili yowawa ndi yotenga nthawi. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Lingilirani Chikhwaya, mmodzi mwa alimi omwe akuchita kuthirira fodya kumunda kuti aphulepo kanthu mvula ikapanda kuchita chilungamo. +Ndikudziweni. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Chikhwaya: Zikavute kumsika Ndine Lingilirani Chikhwaya, mlimi wochokera mdera la Nkhoma mboma la Lilongwe. +Mumalima chiyani? Ndimalima mbewu zosiyanasiyana malingana nkuti masiku ano ntchito ya ulimi njosapanganika. Ukhoza kudalira mbewu imodzi nkugwa nayo osakolola kanthu ndiye potengera upangiri wa alangizi, ndimangobzala mbewu zosiyanasiyana. +Ulimi wanu chaka chino ukuyenda bwanji? Bambo, kunena zoona zinthu zatembenuka. Tayamba kukhala ndi mantha tsopano kuti kodi chikutilonda nchiyani? Chaka chatha mvula sidalongosoke, anthu sitidakolole bwino ndiye pano pomwe timaona ngati mwina chaka chino tipeza polirira, zikuonekanso ngati mavuto ankira mtsogolo. +Ndiye mwangokhala basi nkumadikira chakudza? Ayi, tikuyesetsa njira iyi ndi iyo kuti mwina mbewu zina zipulumuke. Mminda ina tili kale bwinoko chifukwa tidatchingira koma mminda ina monga ya fodya tikuchita kuthirira ndithu ngati ndiwo zamasamba kudimba kuchitira kuti nanga tachoka kale kutali ndipo taononga ndalama, mphamvu ndi nthawi ndiye tikagwere mphwayi pano? Kuli bwino kungodzipereka basi. +Ndiye momwe umakhalira munda wa fodya muja ntchito yake imakhala bwanji? Tidazolowera. Nkale tidayamba ulimi wa fodya ndipo ululu wake tikuudziwa kale ndipo tidauzolowera. Umatheka kugwira ntchito yakalavulagaga chaka chonse nkukakhumudwira kokagulitsa ndiye kuli bwino ulimbe nazo zikamadzavuta kumsika ndi nkhani ina. +Ndiye zimakhala bwanji? Monga ngati ine, munda wanga uli pafupi ndi mtsinje omwe alimi a kuno timagwiritsa ntchito ya mthirira komanso tili ndi sikimu yomwe akatswiri adatiphunzitsa kakololedwe ka madzi ndipo mvula itangoyamba muja tidakololapo madzi. Madzi amenewo ndi omwe tikugwiritsa ntchito pano. Kumunsi kwa mtsinje womwe timadalirawo, tidayamba tautseka kuti madzi asamapite ambiri kupangira kuti mwina mvula ikhoza kutenga nthawi isadayambirenso. +Ndikufuna ndimve za mathiriridwewo potitu munda wa fodya simasewera. +Sitidzipanikiza kwambiri, ayi, timatengako gawo lina lero nkuthirira kenako mawa mbali ina, choncho. Nthawi zina tikakhala ndi nthawi timakathirira mbali ina mmawa madzulonso nkukathirira mbali ina kungofuna kuonetsetsa kuti pomwe mvula izidzabwereranso, fodya adzakhale ali bwino. +Koma muli ndi chiyembekezo chanji pa fodya wanu? Ngakhale nkhawa ilipo komabe ndikayerekeza ndi momwe zikuonekera mminda ya anthu ena, mwina fodya wanga akhoza kudzakhala nawo mgulu la fodya wochititsa kaso chifukwa ngakhale kuli dzuwa chonchi, ayi, masamba ake akuoneka kuti ali ndi mphamvu moti mvula itangoti lero yagwa yambiri, pakhoza kudzuka fodya. +Chaka chatha mvula idachita chimodzimodzi kugwa nyengo yochepa nkudula kenako nkudzagobwera moononga. Pemphero lanu nlotani? Ayi ndithu, pemphero langa nloti zinthu zisakhale choncho chaka chino, Mulungu akadatichitira chifundo. Chaka chatha tidaona zowawa kwambiri chifukwa mbewu zambiri zidakokoloka ndi madzi a mvula osefukira moti chaka chino kuli mavuto, makamaka pachakudya, ndiye timati mwina chaka chino tingaoneko chozizwitsa. +Pezani umuna wa ngombe Nthawi yokhala ndi ngombe za makolo yapita. Ndi K1 500 yokha, alimi akhoza kupeza umuna wa ngombe za makono. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Zonse zikutheka kusukulu ya zaulimi ya Mikolongwe komwe kukupezeka mbewu za ngombe zamkaka za Friesian Holstein. Ndiye palinso mtundu wa nyama ya ngombe zamkaka za Brahman zomwe ndi za mtundu wa nyama ndi mtundu wa Jersey zomwenso ndi za nyama komanso mkaka zimatulutsa wambiri. Malinga ndi yemwe amayanganira nthambi yosunga umuna wa ngombe kusukuluyo, Innocent Mboma, njira yogula umuna ndi yachidule, yosamala komanso yotchipa ndipo alimi akuyenera kutsatira njirayi ngati akufuna mitundu ina ya ngombe. +James Molende kukolola umuna kwa ngombe ya mtundu wa Friesian Madera ambiri kuti ugule ngombe ya mphongo, mtengo wotsikitsitsa ndi K150 000 ngombe imodzi mtengo woti mlimi sangakwanitse. +Nchifukwa chake tikugulitsa umuna kuti alimi asavutike. Umuna wa K1 500 wokha angathe kukakweretsa ngombe imodzi ndipo ndi kamodzi kokha ngombe yatenga bele, adatero a Mboma. Iwo adati umunawu ungakweretsedwe kwa ngombe ya mtundu ulionse ndipo mwana amene akabadweyo akakhala wa mtundu wa umuna omwe adagula. +Kaya ngombe yake ndi ya mtundu wanji, umuna umenewu ukagwirabe ntchito. Ndipo mwana wobadwayo adzatenga bambo ake. +Iye adati umuna umatengedwa Lolemba ndi Lachinayi sabata iliyonse ndipo alimi angathe kupita kusukuluyo tsiku lililonse ndipo umunawo akaupeza. +Pobwera akuyenera kutenga potengera monga fulasiki kuti umunawo usafe. Komanso si kuti alimiwa timangowagulitsa, timawaphunzitsa momwe angasungire komanso momwe angakweretsere ngombe yawo, adatero a Mboma. +Iwo adati patsiku amakolola umuna wochuluka ndi mamililita 10 kwa ngombe imodzi ndipo akaugawa angathe kukweretsa ngombe zazikazi pafupifupi 100. +Kupewa nsabwe za mfodya ndi pano Nsabwe za mufodya ndi gwero limodzi lomwe limachititsa kuti fodya avute malonda kumsika ndipo vutoli likagwera mlimi, chaka chimenecho amalirira kuutsi kaamba koti ngati ogula sadagule fodyayo pamitengo yolira ndiye kuti wabwezedwa. +Malingana ndi katswiri wa zafodya, vutoli ndi lopeweka ndipo kapewedwe kake nkosabowola mthumba poyerekeza ndi zomwe zimalowa pofuna kupulumutsa fodya nsabwezo zikalowa. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mkulu wa bungwe la alimi a fodya la Tobacco Association of Malawi (Tama), Reuben Maigwa, wauza Uchikumbe kuti vuto lalikulu la nsabwe za mufodya ndi lakuti zimateketa fodya nkukhala ngati wagayidwa kale ndiye ukapita kumsika, ogula sachita naye chidwi. +Ogula fodya amayangana mtundu, makulidwe ndi kukhuthala kwa masamba a fodya, osati ufa wa fodya, ayi. Ndiye amati akatsegula belo nkuonamo ufa amaona ngati ndi fodya wachinyengo ndipo amamubweza. Zikatero ndiye kuti chaka chimenecho zadapo, adatero Maigwa. +Iye adati nthawi yopewa vuto la nsabwe za mufodya ndi ino poti ikayambika ntchito yothyola fodya mpata umasowa komanso zimathandiza kuti nsabwezo zisakhale ndi mpata wokwanira oswana. +Mkuluyu adati nthawi zambiri gwero la nsabwezi limakhala zipangizo zomwe zidagwiritsidwa ntchito chaka chinzakecho zomwe zidakhudzidwa ndi nsabwe kapena malo osungiramo fodya panthawi yoyembekezera kupita kumsika. +Tikunena pano, alimi ena adayamba kale kusonkhanitsa zipangizo ngati ziguduli zodindira mabelo, ulusi wosokera ndi zipangizo zina ndipo zimenezi ndizo zimatha kuyambitsa nsabwe ngati komwe zidagwira ntchito mmbuyomo kudali vuto la nsabwe. +Kupewa kwake nkosavuta chifukwa choyenera nkuchapa zipangizo zoterezi bwinobwino nkupopera mankhwala usadasunge pamalo abwino kudikira ntchito yake, adatero Maigwa. +Iye adati kuchapa ndi kupopera kokha sikukwanira ngati malo osungiramowo sali osamalika chifukwa nsabwezo nthawi zina zimatsakamira mmakoma ndiye ngakhale zipangizo zitasamalidwa bwino nkusungidwa mmalo omwe muli nsabwe palibe chomwe chachitika. +Chaka chilichonse malonda a fodya akatha timayenera kutsuka makoma onse a momwe timasungiramo fodya wathu ndi pansi pomwe nkupoperamo makhwala kuti tizilombo ngati nsabwe tife, adatero Maigwa. +Iye adati alimi ambiri amagwa mmavuto ndi nsabwe za fodya kaamba kolekerera nkumaganiza kuti nthawi idakalipo kenako akaona kuti zawakoka manja amayamba kuchita zachidule ntchito nkumaonongeka. +Fodyatu sachedwa, posachedwapa ena ayamba kuthyola ndiye ikangofika nthawi imeneyi mpata umasoweratu chifukwa umati mmawa uli kothyola, masana ukusoka uku ukupachika mmikangala ndiye zoti ungapeze mpata wokachapa ziguduli kapena kukakonza mosungira mpovuta, adatero katswiriyu. +Maigwa adatiso nthawi yomwe ino ndiye yofunika kuyambapo kukonza zigafa ngati zidaonongeka kapena ngati palibiretu kuti pomwe fodya azidzachoka kumunda kubwera kumudzi adzakhale ndi pofikira, osati zomwe amachita ena zopachika fodya mkhitchini mophikira chifukwa chosowa malo osungiramo fodya. +Anatchezera Akundimana Anatchereza, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndakhala pabanja ndi mkazi wanga kuyambira mu 2011. Poyamba zonse zimayenda koma masiku ano ndikamufuna masiku ambiri amanena kuti watopa kapena akudwala. +Ndithu mpaka kumaliza mkonono wabodza. Ndikuganiza kuti ali ndi chibwenzi. Nditani? PB, Phalombe. +PB, Malembo Oyera amaneneratu kuipa kokanizana. Malangizo ambiri a mipingo ina komanso a chikhalidwe amakhala a kuipa kokanizana ngati anthu alowa mbanja. Koma nkhani imeneyi kuthana nayo kwake ndi inu anthu awiri chifukwa zochitika kuchipinda zimathera komweko moti ngakhale ankhoswe sayenera kumalowerera pokhapokha zitafika povutitsitsa. Choncho, muyenera kukambirana pauwiri wanu kuti muone chatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke mnyanga. +Ali kale pabanja Zikomo gogo, Ndili ndi zaka 25 ndipo ndakhala pachibwenzi ndi bambo wina kwa zaka zitatu. Mnzangayo ali pabanja koma amandilipirira lendi nyumba imene ndimakhala ndi mwana wanga yemwe adandipatsa. Vuto ndi lakuti ndikamuuza kuti akaonekere kwathu amakana, komanso kwathu sagona. Nditani poti ndikukula tsopano? NM, Nsanje. +NM, Cholinga cha ubwenzi chachikulu nchakuti Mulungu atalola mudzalowe mbanja. Kodi inuyo pochita chibwenzi ndi munthu wokwatira, cholinga chanu nchiyani? Ngati pali chibwenzi pakati pa munthu wokwatira ndi wina wosakwatira kapena ali ndi mwamuna kwina ndipo akugonana, chomenecho ndi chigololo ndipo ndi tchimo pamaso pa Mulungu; palibe za banja. +Mukanena kuti akukana kukaonekera kwanu, inu mumafuna kuti akadzabwera kudzaonekera kwanu abale anu adzati chiyani? Mudziwe kuti chongobwera kudzaonekera kwanu, ndiye kuti mwamunayo akhoza kukhala ngati wavomereza zodzakukwatirani. Kodi mwamunayo ngakhalenso akwanu angalole izi? Fupa lokakamiza silichedwa kuswa mphika, chimodzimodzinso chikondi sakakamiza. Mwamunayo akuonetsa zizindikiro zoti ngakhale anakuchimwitsa pokupatsa mwana ndipo akukulipirira lendi, za banja ndi iwe sakulingalirapo ata! Udakali wamngono, yangana wina woti ungamange naye banja! Kodi apite? Gogo wanga, Ndatha miyezi iwiri ndi mnyamata amene tikugwirizana zodzamanga banja. Komatu ine ndikadali pasukulu ndipo zatsala zaka zinayi kuti ndimalize. Iyeyo wati andidikira koma wanena kuti zingamuvute kudikira ali kuno ndipo wandipempha kuti abapita ku South Africa. Nkhawa yanga ndi yakuti, nanga atati wapita nkukapeza mkazi wina, zidzatha bwanji? Ndamukondatu kotheratu. Ndimulole apite? JM, Lilongwe. +JM, Kodi ukuganiza kuti atapeza mkazi wina ngakhale ali konkuno sangatengane naye poona kuchedwa? Izi ndanena chifukwa zomwe akunena kuti apite ku South Africa kaye likhoza kukhala ganizo labwino. Iyeyo utamulola kuti apite ku Joni iwe nkumaliza sukulu ndiye nkupezeka kuti wakutaya mnjirayi ungadandaule chiyani? Zikhozatu kutheka kuti iyeyo akhoza kukhala konkuno, molephera kupirira iwe nkupezeka wapatsidwa mimba tsono zidzakuthandiza chiyani? Mulole apite, chifukwatu zikhozanso kuthandiza kumanga maziko a banja lanu ngati muli oganiza bwino. Chachikulu nchakuti inu nonse muyenera kudziwa kuti sakupita ku Joniko kukatayitsa nthawi koma kukakonza maziko a banja lanu, monga iwenso ukuchitira popita kusukulu. +Amandizunguza Anatchereza, Ndidamangitsa ukwati mu 1997 ndipo ndili ndi ana atatu koma mwamuna wanga amandizunza. Ngakhale ndidwale, palibe chimene amachitapo. Komatu ine kwawo ndiye ndimapita pakakhala kalikonse. Mwamuna wangayo ali ndi ana awiri kuchibwenzi. Ndikathetse ukwati kukhoti kapena? MJT, Lilongwe. +Osolola ndalama za Edzi mitima ili phaphapha! Unduna wa zaumoyo wati zotsatira zakafukufuku wokhudza kusokonekera kwa ndalama zothandizira kulimbana ndi matenda a Edzi zatuluka, koma undunawu ukudikira ndemanga za nthambi yoona zakapewedwe ka matenda ya Centre for Disease Control (CDC) kuti unene tchutchutchu wake. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mlembi wamkulu mu undunawu, Macphail Magwira, watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati zotsatirazi azitulutsa mtsogolo muno nkuwona kuti undunawu ungachitenji ndi anthu omwe akukhudzidwa ndi kusokonekera kwa ndalamazi. +Zotsatira za kafukufuku zatulukadi koma zili mmanja mwa nthambi yoona zakapewedwe ka matenda osiyanasiyana kuti nawo aikepo ndemanga zawo. Zikachoka kumeneko, mpomwe tione kuti tingatani potengera zotsatira ndi ndemangazo, adatero Magwira. +Iye adati pa anthu oganiziridwa onse, omwe adzapezeke olakwa adzaimitsidwa ntchito chifukwa chosokoneza ndalama za boma. +Kumapeto kwa chaka chatha, unduna wa zaumoyo udaimitsa ntchito anthu 63 zitadziwika kuti ndalama zina zomwe zimayenera kugwira ntchito yolimbana ndi matenda a Edzi zasokonekera ndipo undunawu umafuna nthawi ndi mpata wofufuzira. +Tidaimitsa anthu ena omwe amaganiziridwa nawo. Ena mwa anthuwa amagwira kunthambi yowerengera ndalama za undunawu, makalaliki ndi ogwira ntchito mmaofesi ena kuti tifufufuze bwinobwino popanda zopinga, adatero Magwira. +Anthuwa adapatsidwa mpaka pa 31 March chaka chino ngati tsiku lomwe angadzayambe ntchito koma mpaka pano anthuwa sadayambebe ntchito kudikira kuti zotsatira za kafukufukuyo zituluke. +Maunduna ndi nthambi zina za boma zakhala zikukhudzidwa ndi kusokonekera kwa ndalama za boma zomwe ena amangoti Kashigeti pofanizira ndi kubedwa kwa ndalama zankhaninkhani kulikulu la boma. +Auka atatha zaka 11 mmanda ku ntchisi Pa 16 April 2005 lidali tsiku lachisoni mmudzi mwa Ngwanje, T/A Malenga mboma la Ntchisi pomwe mayi Nkomanyama Charles adamwalira akubereka mwana wake wa nambala 6. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Zaka 11 chichitikireni izi, zodabwitsa zaoneka mmudzimo pomwe munthu amene akumuganizira kuti ndi malemuyo adapezeka ali zungulizunguli mmphepete mwa phiri la Katsumbi mawa wa pa 13 February ali moyo. +Mneneri wa apolisi mbomalo Gladson Mbumpha, watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati pano mayiyo ali kwa amene akuti ndi makolo ake. +Anthu akukhamukira ku Ntchisi kukaona Nkomanyama Malinga ndi Mbumpha, apolisi adali amkhalapakati wa zokambirana pakati pa mafumu ndi makolo a mayiyo kuti amulandire. +Poyamba mayi ake omwe ndi a mmudzi mwa Chithonje ankachita naye mantha moti ankasungidwa ndi mfumu Katipwiri kufikira titamaliza zokambirana pa 15 February, adatero Mbumpha. +Mayiyo atangopezeka, yemwe akuti ndi mwamuna wake, Yobu Gwaza, wa mmudzi mwa Ngwanje, ndiye adayamba kumuzindikira ndipo adafotokoza kuti mkazi wakeyo adamwalira mchaka cha 2005 akubereka Dorica, mwana wawo womaliza yemwe ali moyobe mpaka pano. +Iye adati adalera yekha mwanayo ndipo chithunzithunzi cha mkazi wakeyo chidali chikadali mmutu nchifukwa chake sadachedwe kumuzindikira atamuona. +Gwaza adati alibe vuto lililonse ndi mkazi wakeyo ndipo ndi wokonzeka kumulandira akapeza thandizo nkubwerera munzeru zake bwinobwino. +Ngati angachire nkukhala bwinobwino chomuletsera kubwerera pakhomo pake nchiyani? Mmesa ana ake ali kunyumba komweko? adatero Gwaza. +Anthu akukhamukira kukaona zozizwitsazo, ye,we akuti ndi malume a mayiyo, Masaiti Kalulu, atabweretsa chithunzi chomwe Nkomanyama adajambulitsa asadafe ndipo anthu omwe adachiona kuphatikizapo apolisi akuti pali kufanana pakati pa nkhope ya pachithunziyo ndi mayiyo. +Mbumpha adati anthuwo ataona chithunzicho adakwiya ndi kukana kwa mayi a woukayo ndipo pamalopo padayamba phokoso lomwe adakaletsa ndi apolisi. +Padali chisokonezo moti chipanda apolisi kufika msanga, pakadachitika chachikulu mwinanso mpaka mayiyo akadamenyedwa, adatero. Padakalipano mayi akumuganizira kuti adaukayo ali kwa mayi ake koma akuti sakutha kuyankhula komanso nthawi zina amadya mwachidodo. +Tikukhala naye bwinobwino ngakhale kuti pena amachita zinthu mwachidodo monga kudya. Akhoza kuyamba pano koma kuti amalize pakumatenga nthawi. +Vuto lina lomwe lilipo ndi losatha kuyankhula ndiye nzovuta kudziwa chomwe akufuna. Tiona kuti akhala bwanji tikayenda naye, adatero mayi Charles. +Mfumu Chithonje ya mmudzi momwe mumachokeratu makolo a mayiyo idatsimikiza za maliro a mayiyo ponena kuti ngoziyo itachita mchaka cha 2005, idalandira uthenga ndipo idachita nawo mwambo wa malirowo. +Mfumuyo idati kawirikawiri nkhani zokhudza munthu womwalira nkupezeka ali moyo zimazunguza mutu ndiponso zimayambitsa phokoso anthu akazitengera pamgongo. +Pakalipano apolisi alangiza mafumu ozungulira derali kuti aphe tsiku kupita kukanda kuti akatsimikize ngatidi mmanda momwe adaika mtembo wa Nkomanyama Charles mulibedi thpi lake. +Mkulu wina wa mpingo wa Church of Christ mboma la Nkhotakota, Maxwel Nangunde, adati amakhulupirira kuti munthu akamwalira basi kwake kwatha mpaka patsiku la chiweruzo. +Zina ukamva abale koma mpovuta kunena kuti chenicheni nchiti chifukwa anthufe timakhulupirira kuti munthu akapita wapita basi mpaka tsiku la chiweruzo, adatero Nangunde. +Koma mmbiri ya chilengedwe tikumva za kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu amenenso adaukitsapo anthu angapo monga Lazalo, mwana wa Jairus kudzanso mnyamata wina wa mayi wamasiye ku Nain. +Tikumvanso kuti pamene Yesu adapachikidwa pamtanda, adaukanso patapita masiku anayi ndipo adalowa mlimbo naukitsa matupi a anthu abwino omwe adafa. +Komanso mbuku la chipangano chakale tikuwerenga za mmene mneneri Eliya adaukitsira mwana wa namfedwa wa Zarephath; Elisha naye adaukitsa mwana wa mkazi wina Mshunammite kwa akufa. +Naye Paulo akuti adaukitsikwa kwa akufa atagedendwa ndi miyala ndi anthu a ku Antioch ndi Iconium nkumusiya ali thapsa! Komanso Paulo yemwenso akuti adaukitsa Eutychus yemwe adafa atagwa pansi kuchokera panyumba yosanjikizana mmene ankatsinza. +Petulo nayenso adaukitsa mayi wa ntchito zabwino dzina lake Tabitha wa ku Joppa, yemwe amatchedwanso kuti Dorcas, atamwalira nkuikidwa mmanda. +Kulakwa, kulakwatu pa Wenela! Tsikulo lidali lokumbukira asungwana ndi amayi oyendayenda ndipo tidazunguliradi mumzinda wa Lilongwe. Tidali ndi Abiti Patuma kuti ationetse monse. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kudalitu kuyenda, kuzungulira apo akuti pa Matchansi (kaya ndiye kuti chiyani), kukafika uko ku Culture Club, komanso uku kwa Biwi, mpaka komwe ku Chigwirizano ndiponso pa Bwandiro, inde paja pa Ma China komanso ku Likuni ndi Chigwirizano sikuti tidaphonyako. Mukanena za Bwalo la Njovu ndiye osanena, apo pa Akazembe komanso hotela yopanda zipinda zogona ija, ndiye osaiwala mmwamba muja mumakhala anthu odikira kukwera Taqwa ngakhalenso a nsomba. Lilongwe! Nanga ndikuuzeninso kuti tidafika ku Mzuzu? Pa Dziwazako zidalipo! Nanjinanji pa Sports Caf! Eisssh, uku ku Mlambe Inn ndi Paris Club! Kudalitu kuyenda. Mpaka tidafika ku Chitipa. Kumenekotu Moya Pete amatsegulira mpita. Nanga inu mumayesa ndinatsala mu Lilongwe? Mwandiona chiyani? Ndipo kumenekonso sitidakhaleko nthawi. Tidabwerera kwathu ku Wenela. Pajatu kwathu kudasintha, si kwa Kanduku! Kwathu nku Wenela. +Chongofika pa Wenela, tidapeza mkulu wina akunena kuti wangochoka ku Lilongwe kumene mkulu wachikwama amabwebweta izi ndi izo zachuma. Kodi mkulu ameneyu sanatopebe? Kodi iyeyo, chikwama ichi timaona atanyamula chaka ndi chaka sichimulemera? Nanga bwana wamtundu wanji wopanda chola boyi? Bwana wamtundu wanji kupanira bulifikesi, kapena mwati ndi sutukesi? Nanga amakanenanji? Amanena chiyani uyu mdala? Zaka zitatu akuyankhula zosamveka koma timagoti komabe! Ndinaiwala. Titafika ku Chitipa, tidamva kuti Moya Pete wati Kamacha wapita ku Tanzania kukaphunzira za momwe tingagwirire awa akupha abale anzathu achialubino! Kulakwa. +Nanga akaphunzirako chiyani? Akatenga chiyani? Kodi mmesa kalelo tinkati ankangosowa? Kulakwa. +Kudya posalima. +Kulakwa. +Nanga izi zoletsa asinganga zadza ndi yani? Kodi nkhaniyi ndi ya unganga? Adafika mnyamata wina pa Wenela ndi chikwama chake. Adandiitanira pambali. +Akulu, ndikufuna kuchita nanu bizinesi. Tikudziwa muli ndi 15 mita. Tikangopeza mafupa a 10 mita, inutu muyiphula! Tikagulitsa 50 mita pena pake, adatero. +Zabwino. Koma ndimufunse kaye Abiti Patuma, ndidamuuza. +Kulakwa. +Kulakwa. +Kodi iwe sukudziwa kuti awawa ali ngati aja ankagulitsa mankhwala osambitsira mahatchi? Sukudziwa kuti iwowa ali ngati aja ankagulitsa diamond mtauni ya Blantyre ndi Lilongwe? Sukudziwa kuti awa ndi anyamata a chintambalala? Apolisi akuwadziwa kale anyamatawa nanga mpaka kupita dziko lakuti likufuna kutilanda nyanja? Ndipo mwati chaka chino sindilandira feteleza? adatero Abiti Patuma. +Ndaziona: Aona kuwala ku Mozambiki Mwezi wathawu osewera awiri, Ndaziona Chatsalira ndi Green Harawa adachoka ku Silver Strikers ulendo ku Mozambique kukasaka moyo wina. Chatsalira wauza BOBBY KABANGO kuti ku Mozambique kuli mkaka ndi uchi ndipo wayamba kumva kukoma. Zakoma bwanji kodi? Kucheza kwawo kuli motere. +Ali ku Mozambique: Chatsalira Wawa mbale wanga, zikuyenda kumeneko? Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Inde achimwene. Ku Malawi kuli bwanji? Pangono, chimanga chikusowa, kaya kumeneko? Kuno tonse tilipo, ine ndi mnzanga Green Harawa zonse zikuyenda ndipo pagalaundi zonse zili bwino. +Chili bwino nchiyani? Mukudziwanso kuti timu ya Ferroviarrio de Nampula si timu yaingono, ndiye ukamapatsidwa mpata kuti uonetse luso lako anthu ndi kumayamikira zimatanthauza zambiri. +Kodi ligi yanu iyamba liti? Iyamba mu March moti zokonzekera zili mkati. Panopa tili mnjira ulendo ku South Africa kukachita zokonzekera koma matimu amene tikukasewera nawo sadatiuze. +Zokonzekera zikuyenda bwanji? Zonse zili bwino, tachita nawo zokonzekera kwa sabata ziwiri, anthu akuyamika. +Wachita chiyani kuti ayamikire? Zigoli, ndakoleka kale zigoli 10. Nayenso Harawa wachinya 15 ngati sindikulakwa. +Ukusewera malo ati kuti mpaka uchinye zigoli 10? Pakati cha kumanzere pena kumanja koma mokagundagunda pagolo. +Kumeneko ndiye ukutchedwa ndi dzina liti? Da Silva Chatsalira chifukwa ndikuvala jersey nambala 21. Mukudziwanso kuti ndimakonda da Silva wa Manchester City. +Ndalama mukulandira motani? Malipiro ali bwino kwambiri koma sindinganene momwe tikulandirira. Chilichonse chokhudza mpira kuno chili bwino kusiyana ndi kwathuko. Mbali zonse tingonena choncho kuti zili bwino kuyerekeza ndi kumudziko. +Kuphana kwaphweka pa Wenela Tsiku limenelo diraiva wina adati ndikhale kondakitala wa ganyu paulendo wake wolowera ku Machinjiri. Nkhani zinkakamba anthu mmenemo zidali zachilendo kwa ine. +Namwino wina, amene adatsika pa Magalasi ankanena za kachilombo koopsa ka Zika kamene kakuchititsa ana ena a ku Brazil azibadwa ndi mitu yaingono zedi. Nthenda zachilendo zachuluka. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kuchoka apo, namwinoyo ankakamba za mankhwala oopsa otchedwa polonium-210. Ameneyotu ndi poizoni woopsa amene wapha anthu ena otchuka. Asayansi akuti poizoni woopsayu akupezekanso mufodya yemwe ena amakwemba, adapitiriza chiphunzitso namwinoyo. +Abale anzanga, ine nkadatolapo chiyani? Kwa ine kudali kutolera ndalama ndi kutseka chitseko. +Chongoti mayi uja tsikeni, nkhani zidasintha. +Abale, koma tikuphana udyo. Chikuchitika nchiyani? Nkhani ingonongono basi wina wafapo, adatero bambo adakhala mpando wakutsogolo. +Ndi chiyani koma? Ku Machinjiri kwathuku, miyezi iwiri yapitayi nkhanizi ndiye zosayamba. Wantchito wapanja wina paja adapha wantchito wamnyumba nkuthawa ndi matumba atatu a chimanga. Wabizinesi wina wapha wabizinesi mnzake ndipo wina ndi uyu adapezeka ataphedwa nkuchotsedwa maso ndi nkhope. Zoopsa, adayankhira wina. +Si ku Machinjiri kokha. Mwaiwala za bambo wa ku Zingwangwa woombera mkazi ndi mwana wake nkudziphayu? Nanga mwana wa ku Mulanje wapha mayi ake nkuwakwirira mnyumba ati chifukwa amamudzudzula kuba? mtsikana wina amene adavala yunifomu ya sukulu ya za hotela adatero. +Nanga uyu bambo wopha mkazi wake atapeza mauthenga a foni amene amakaikira kuti mkaziyo amatumizira bwenzi lake chonsecho mauthengawo adali a mngono wa mkaziyo yemwe adabwereka foni. Nchiyani chatigwera? adafunsa mkulu wake atanyamula majumbo mosaona zoti ndi pakati pa January. +Mawu anu ali mkamwa, simunamve za mzimayi wapezeka ataphedwa mnyumba yogona alendo ku Bangwe? adafunsa diraiva. +Ndidaikira mangombe: Nanga za mkulu wotuma zigandanga kukapha mkazi wake wakale uja bwanji? Abale anzanga, ndisaname, izi zikundipatsa mantha. Thupi lamera tsemwe. Moyo wa munthu uli mmanja ndithu. +Mungayembekeze zotani mdziko limene mukunena kuti anthu ophwanya malamulo ena asamamangidwe? Poyamba ndimayesatu akadachotsa kaye lamulolo kusiyana ndi kuti ophwanya lamulo asamamangidwe, kapena akamangidwa azitulutsidwa, adatero mkulu wina. +Zoona. Anthutu ogonanana ndi abale awo alipo muno. Tsono akayamba kubwera poyera kuti nawonso alipo ochepa kwambiri ndipo ndi chilengedwe chawo kutero choncho kuwamanga nkuwaphwanyira ufulu. Chipwirikiti chobwera chikhala chotani? adafunsa mzimayi adayandikana naye. +Aliyense mbasimo adangoti duu! Diraiva adatsegula wailesi pomwe aliyense amalingalira za nkhanizo. Padali Moya Pete. Adali maganizo athu kuti Moya Pete akambapo kanthu pa zakuphana chisawawa kukuchitikaku. +Koma ayi. +Yesu anati akakumenyani khofi mbali iyi, mupereke linali. Otsutsa ndi a mabungwe mwandimenya mbali iyi ndakupatsani tsaya linali. Tsono Yesu sadanene kuti mukandimenyanso khofi lina ndichitenji. Mwandimenya katatu tsono ndiona umo ndingachitire, adatero. +Mkulu wina adaseka chikhakhali. Kodi ndimayesa Yesu adati munthu akakulakwira ka 539 uyeneranso kumukhululukiranso ka 539, adatero iye. +Miyambo ya ukwati Ukwati sangotengana ngati nkhuku, pali miyambo yake. Ukalakwitsa miyamboyi, mavuto ena akakugwera umasowa mtengo wogwira. Pakati pa Achewa miyambo ya ukwati nayo ilipo. KONDWANI KAMIYALA adacheza ndi Chikumbutso Funani wa mmudzi mwa Phulusa kwa T/A Kasumbu ku Dedza kuti atambasule zoyenera kutsata. Adacheza motere: Akulu zikuyenda? Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Zikuyenda pangonopangono, mavuto a zachuma omwewa basi. +Funani: Kukagwa maliro ungasowe mtengo wogwira Ndaona mukuchita izi za kabanza. Chiyambire ntchito ndiyomweyi? Ayi ndithu. Ndidakagwirako ntchito ku famu ina ku Ntchisi. Ndidagwira kwa chaka chimodzi ndipo nditalandira malipiro anga a pachaka, K47 000, ndidabwerera kumudzi kuno. Ndidagula njinga ndipo ndakhala ndikuchita izi kwa zaka ziwiri. +Maphunziro mudapita nawo patali bwanji? Ndidalekeza sitandade 7 pasukulu ya Chipaluka. Mudziwa zovuta za kuno kumudzi. +Zovuta zanji? Makolo ambiri amakakamiza ana awo kuti aleke sukulu azikawathandiza kumunda kapena kupita kuphiri kukasaka nkhuni. Pofuna kuti tisaone kuzunzika kotero, ambiri timasiya sukulu nkukakwatira kapena kukwatiwa kuti tizidzipangira tokha zapakhomo. Ana ena akukwatira ali ndi zaka 15! Tsono miyambo ya ukwati imayenda bwanji kuno? Kunotu kumakhala kupereka chapamudzi komanso ya chitengwa. Komanso kuli chiwongo, chamsana chimene madera ena amati malowolo komanso pamakhala nkhuku. +Tafotokozani poyamba za chapamudzi ndi chamsana. +Chapamudzi ndi ndalama zimene zimaperekedwa ngati mwamuna akufuna kukhala mkamwini mmudzi. Ndalamayi imapita kwa mfumu. Chitengwa ndiye umapereka kwa mfumu pamene ukutenga mkazi mmudzi kuti ukakhale naye kwanu. +Kodi mitengo yake imasiyana? Eya imasiyana. Mwachitsanzo, padakali pano chapamudzi ndi K7 000 pomwe ya chitengwa ndi K5 000. +Cholinga choperekera kwa amfumu nchiyani? Iwo chikuwakhudza nchiyani pamene anthu awiri akondana? Musatero. Kodi utangobwera nkukwatira mmudzi amfumu osadziwa powapatsa chapamudzi utamwalira mwambo wa maliro ungayende bwanji? Nanga utatenga mkazi kupita naye kwanu amfumu osadziwa chifukwa sunawapatse ya chitengwa, mkaziyo nkumwalira mwambo wa maliro ukhala wotani? Mfumu imakana kuti sitikudziwa kuti tili ndi mkamwini kapena mkazi wakuti ndi nthengwa mmudzi wina. +Kodi mudachita kupita kwa mfumu kukapereka ndalamayo? Ayi. Mwa mwambo wake, tidapita kwa eni banja. Pamtundu wa chifumu amasankha munthu mmodzi amene amatchedwa mwini banja. Tikapereka kwa iwo ndiwo amakapereka kwa mfumu. +Tsono munakamba za chiwongo, chamsana komanso nkhuku. Tatambasulani. +Chiwongo chimaperekedwa ngati kuthokoza kuti mkazi adaleledwa mpaka kukula. Dziwani kuti liwu loti chiwongo limatanthauzanso mfunda umene amayi amakhala nawo. Mwachitsanzo, mwana wamkazi wa Obanda chiwongo chake ndi Nabanda. Tikakamba za chamsana kapena malowolo ndiye amaperekedwa kwa mayi a mkazi. Nkhuku ndiye ndi ija amagawana ankhoswe. +Kodi anthu akuzitsatabe? Alipo ambiri amene akutsata. Koma nthawi zina ena satsatira izi chifukwa mitundu ya sakanikirana. +Milandu ya maalubino Izipita kukhothi lalikulu Milandu yokhudza kuphedwa kapena kusowetsedwa kwa maalubino tsopano akuti izikakambidwira mukhothi lalikulu lomwe lili ndi mphamvu yopereka chilango chokhwimirapo kuposa khothi la majisitireti lomwe chilango chomwe lingapereke nchochepa, Msangulutso utha kuvumbula. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Milanduyi sizitengera kuchepa kapena kukula kwake pofuna kuteteza maalubino, omwe miyoyo yawo ili pachiswe kaamba ka zikhulupiriro za anthu ena zoti mafupa ndi ziwalo za anthuwa ndi zizimba za mankhwala olemeretsa. +Mneneri wa nthambi ya makhothi Mlenga Mvula wati ngakhale sadalandire kalata yotsimikiza izi, makhothi angonoangono a majisitireti ndi ovomerezedwa kusamba mmanja pankhani zotere kuti nkhothi lalikulu ligwire ntchito. +Sindidalandire kalata iliyonse pankhani imeneyi koma kutengera momwe zinthu zilili pankhani yokhudza maalubino, mamajisireti ndi omasuka kusamba mmanja pamilandu yokhudza maalubino kuti khothi lalikulu ndilo limve ndi kupereka chigamulo ndi chilango, adatero Mvula polankhula ndi Msangulutso Lachitatu lapitali. +Bwaloli tsopano lizizenga milandu yokhudza maalubino Iye adati mndondomeko za makhothi, khothi lililonse lili ndi mlingo womwe silingabzole popereka chilango ndiye potsatira madandaulo a anthu kuti kuzunza maalubino kukunka mtsogolo kaamba ka zilango zochepa, nkofunika kuti khothi lalikulu ndilo lizizenga milanduyi. +Majisitireti sangapitirire mlingo wina wake popereka chilango, ndiye kutengera zilango zomwe anthu akufuna kuti ozunza maalubino azilandira, majisitireti akuyenera kutumiza mlanduwo kukhothilalikulu, adatero Mvula. +Chitsanzo cha nkhaniyi chapezeka ku Mchinji komwe majisireti Rodwell Mejja Phiri wasamba mmanja pamlandu wa Zione Gabina Kamngola, wa zaka 25, yemwe akuzengedwa mlandu womuganizira kuopseza msuweni wake, Gertrude Ulaya, wa zaka 22, yemwe ndi wachialubino. +Mneneri wa polisi ku Mchinji, Moses Nyirenda, wati Kamngola akumuganizira kuti adanena msuweni wakeyo kuti iye ndi ndalama ndipo akadakhala mwana wake akadamupha. Nkhaniyi akuti idaopsa msuweni wakeyo ndi mayi ake, Mary Ulaya, omwe adakadandaula kupolisi. +Iye adati apolisi atafufuza za nkhaniyi, adatsegulira Kamngola mlandu woopseza munthu ndi mchitidwe womwe ungayambitse chisokonezo. +Malinga ndi Nyirenda, majisitireti Mejja Phiri adanena kuti nkhaniyo idamukulira malingana ndi mlingo wa chilango chomwe angapereke ndipo mmalo mwake adapereka kalata ya limandi ndipo mayiyo ali ku Maula kuyembekezera kukaonekera kukhothi lalikulu ku Lilongwe. +Titamufunsa ngati sikumulakwira wozengedwa mlandu waungono ngati uwu kumutumiza kubwalo lalikulu mlandu wake usanazengedwe kubwalo la majisitireti, Mvula adati pakhothi lililonse, munthu amalandira chilungamo mofanana chifukwa mbali zonse ziwiri zokhudzidwa zimakhala ndi mpata wonena mbali zawo ndipo chigamulo chimachokera pa zokamba zawozo. +Zilibe kuti ndi khothi la majisitireti, khothi lalikulu kapena la Supreme, ayi. Kulikonse mbali zokhudzidwa zimapatsidwa mpata wonena mbali zawo ndipo chigamulo chimachokera pamenepo, adatero Mlenga. +Iye adatsindika kuti nkhani yaikulu yagona pokhwimitsa chitetezo cha maalubino kuti anthu akaona zilango zikuluzikulu zomwe zikuperekedwa ayambe kukhala ndi mantha ndipo mchitidwe wozunza maalubino uthe. +Potsirapo ndemanga, katswiri wa zamalamulo kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College, Edge Kanyongolo, adavomereza kuti mlandu wotere ndi mlandu waungono woyenera khothi la majisireti, koma zikutengera mfundo zomwe iye wagwiritsa ntchito posamba mmanja. +Umenewu ndi umodzi mwa milandu ingonoingono potengera malamulo ogamulira milandu ndipo umayenera kugamulidwa ndi majisireti chifukwa chilango chake nchochepa. Ngakhale zili chonchi, zimatengera kuti iye wawonaponji pankhaniyo chifukwa pazifukwa zina akhoza kuutumiza kukhothi lalikulu, adatero Kanyongolo. +Naye mlembi wa bungwe la maloya Khumbo Soko adagwirizana ndi kanyongolo ponena kuti majisitireti aliyense ali ndi mpata wofunsa chiunikiro cha khothi lalikulu ngati akuona kuti nkhaniyo ikuposa mphamvu zake. +Posamba mmanja pa mlanduwo pa 3 June, 2016, Mejja Phiri adati adauzidwa kuti milandu yonse yamtunduwu aziitumiza kukhothi lalikulu kuti anthu opezeka olakwa azilandira chilango chokwanira. +Gawo 88 (1) la milandu ndi zilango zake yokhudza mlandu woopseza munthu ili ndi magawo awiri omwe kaperekedwe ka chilango chake nkosiyana. +Mlandu woopseza womwewu, munthu akhoza kumangidwa mpakana moyo wake wonse ngati adatchulapo za kupha, pomwe ngati adangoti ndikumenya poopsezapo, chilango chachikulu chomwe angalandire ndi zaka zitatu kundende, adatero Nyirenda. +Iye adati chokhacho chotchula kupha ndi kutengera kuti woganiziridwayo adaopseza munthu wa mtundu womwe dziko lonse lapansi likudandaula kuti uli pachiwopsezo chachikulu ndi mlandu waukulu. +Tame Mwawa: Phwete ndiye kudya kwake Sewero la Tikuferanji ndi limodzi mwa masewero omwe amapereka phunziro kwa anthu pazochitika mmoyo wa tsiku ndi tsiku komanso ndi msangulutso kwa anthu ambiri. Seweroli limaonetsedwa pakanema komanso kumveka pawailesi ya MBC. STEVEN PEMBAMOYO adachita chidwi ndi mmodzi mwa omwe amachita nawo seweroli, Tame Mwawa, yemwe ambiri amamudziwa kuti Chiphwanya museweromo ndipo adacheza naye motere: Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mwawa: Ndidabadwa wazisudzo Ndikudziwe mnzanga. +Ndine Tame Mwawa ndimakhala ku Machinjiri ku Blantyre koma kwathu nku Chiradzulu mmudzi mwa Kambalame, T/A Mpama. +Udabadwa mchaka chanji? Ndidabadwa pa 26 October, 1977 ndipo ndine woyamba mbanja la ana 7, amuna 5 ndi asungwana awiri. +Mbiri yako pazisudzo ndi yotani? Ndikhoza kunena kuti ndidabadwa wazisudzo kale. Abale anga amandiuza kuti ndili wamngono ndikadziongola kapena ndikamalira anthu amandiunjirira nkumaseka ndipo makolo anga adadziwiratu kuti ndidzakhala msangalatsi. Kusukulu anzanga ngakhalenso aphunzitsi ankachita kudziwa kuti Tame wabwera zilango ndiye zidali zosatha. Nthawi zina ndinkalembedwa pa anthu olongolola koma pomwe sindidapite kusukulu nkomwe. Pachikondwerero chokumbukira ufulu wa dziko ndinkapanga nawo zisudzo ndipo malipiro ake adali Fanta ndi mpunga wa nyama. Ndinkapanganso sewero la Ambuye Yesu. +Udapezeka bwanji musewero la Tikuferanji? Nthawi ina yake ankakajambula seweroli pafupi ndi kwathu ndiye penapake pamafunika singanga koma munthu amasowa tsono ine ndidadzipereka kuti ndiyesere nkuchita bwino basi kulowa mseweroli kudali kumeneko. Panthawi imeneyo ndidadziwana ndi akuluakulu ena azisudzo monga Frank Yalu (Nginde) yemwe adanditenga kukalowa gulu lake la zisudzo lotchedwa Kasupe Arts Theatre. Pano ndidadziwika kwambiri moti ndimapezeka mmagulu azisudzo osiyanasiyana monga Kwathu komanso mumafilimi osiyanasiyana. Imodzi mwa mafilimu omwe ndilimo ndi ya Chinganingani yomwe ikuoneka pakanema ya Malawi komanso ndidayambitsa nawo pologalamu ya Phwete pa kanema yomweyi. Pawayilesi ndimapanga nawo Sewero la Sabata Ino. +Dzina la Chiphwanya lidayamba bwanji? Kumudzi kwathu ku Chiradzulu kuli mkulu wina dzina lake Chiphwanya yemwe ndi wolongolola komanso wosachedwa kupsa mtima ndiye nditaona malo omwe ndimapatsidwa mmasewero ambiri ndidaona kuti dzinali ndi londiyenera. +Nzoona kuti pakhomo pako udadzala zikho zambiri? Eya, ndimadziwiratu mbali zomwe anzanga amakonda kundipatsa pazisudzo motero ndidadzala zikho zambiri komanso mikanda pakhomo panga ili mbweee! Moti anthu ena amaona ngati ndimapangadi zausinganga. +Taphulanji mzaka 52? Anthu komanso atsogoleri ena ati zaka 52 za ufulu wodzilamulira zomwe dziko la Malawi lidakwanitsa Lachitatu ndi nthabwala chabe chifukwa zinthu zanyanya kusiyana ndi kale. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Anthuwa amalankhulapo kumbali ya momwe ndale zikuyendera, chuma, maphunziro komanso ulamuliro wabwino mzaka 52 zomwe zapita. +Mkulu wa bungwe loona zamaphunziro la Civil Society Education Coalition (CSEC) Benedicto Kondowe wati zomwe Malawi wakwaniritsa mzaka 52 kumbali ya maphunziro, maiko ena azichita mzaka 20 zokha. +Iye wati kumudzi komwe kumakhala anthu ambiri, zinthu sizili bwino ngakhale tikusangalala kuti takwanitsa zaka 52 zodziyimira patokha. +Pitani ku Chikwawa, sukulu zina kuyambira sitandade 1 mpaka 8 ana ali ndi mphunzitsi mmodzi. Pitani ku Dedza, mphunzitsi mmodzi akuphunzitsa ana 400. Zomwezi mukazipezanso ku Rumphi. +Amalawi kulimbirana chimanga nthawi ya njala Ana akuphunzirabe pansi pa mitengo apo ayi ndiye kuti ndi mchisakasa chomwe makolo amanga. Kodi izi zikutanthauzadi kuti takwanitsa zaka 52? adafunsa Kondowe. +Iye adati ku Angola, mphunzitsi mmodzi akuphunzitsa ana osaposa 45 pamene ku Malawi mphunzitsi mmodzi akuphunzitsa ana oposa 100 zomwe wati maphunziro akulowa pansi mmalo moti asinthe. +Ku Mozambique, Zambia ngakhale Zimbabwe, sitingafanane nawo. Ndikuchokera ku Machinga komwe ndidaona mphunzitsi akuphunzitsa ana oposa 400 yekha. Kodi zaka 52 zili ndi tanthauzonso pamenepa? adazizwa Kondowe. +Iye adati chomwe angaloze kumbali ya maphunziro ndi chiwerengero cha ana amene akupita kusukulu komanso kupezeka kwa sukulu mmadera ambiri zomwe ndi nkhani yabwino. +Kumbali ya ndale, mphunzitsi wa ndale kusukulu ya Chancellor Collage Joseph Chunga wati palibe chomwe angaloze koma mavuto okhaokha. +Ngakhale Chunga akuti palibe angaloze, dziko lino lili ndi zipani zambiri zoposa 50 pamene kale kudali chipani chimodzi chokha. +Izi si zoti mungamaloze kuti ndale zikuyenda bwino chifukwa tili ndi zipani zambiri. Ndikutero chifukwa mukadzifunsa mupeza kuti zipanizo zikuyambidwa chifukwa cha kusamvana komwe kwabuka mchipani ndipo mulibe kulolerana, mapeto ake ndi kukayambitsa chipani chawo. Ndiye uku ndi kutukuka? Komanso ngakhale zipanizo zikufika 50, ndi zipani zingati zomwe zikuoneka? Mupeza kuti nzosaposa zisanu, adatero Chunga. +Iye adaonjeza kuti dziko la Malawi adati mlozo wina kuti zinthu sizikuyenda pa ndale zikuonekera pomwe mtsogoleri akangochoka pampando, umakhala ulendo wa mchitokosi. +Poyankhapo pa momwe zinthu zikuyendera mdziko muno, womenyera ufulu wachibadwidwe, Billy Mayaya wati atsogoleri athu ndiwo asokoneza zinthu kotero akuyenera kuchotsedwa. +Iye wati mavuto akhodzokera ndipo mmalo mopita patsogolo, zinthu zikubwerera mmbuyo, zomwe wati zikuchitika chifukwa cha atsogoleri. +Dziko limayenda bwino ngati anthu akupeza mwayi wa ntchito, anthu akukhala ndi ndalama komanso ngati anthu akukwezeredwa ndalama mmalo amene akugwirira ntchito. Izi mdziko muno ndi vuto lalikulu, ntchito zikusowa komanso anthu sakukwezeredwa malipiro. +Zinthu zasokonekera ndipo zonsezi ndi atsogoleri amene tidawasankha kuti akonze zinthu, ndiye ngati zinthuzo sizikukonzedwa, ndi bwino kuwachotsa kuti pabwere ena amene angatithandize, adatero Mayaya. +Kunyadira ufulu wodzilamulira Dziko la Malawi lidalandira ufulu wodzilamulira pa 6 July 1964 kuchokera ku ulamuliro wa atsamunda a Chingerezi. Lachitatu lapitali, timakumbukira kuti patha zaka 52 kuchokera pomwe tidayamba kudzilamulira. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi mikoko yogona Moses Malunga ndi Mustaf Mbewe za mbiri ya ufulu wathu. Adacheza motere: Ndiyambe ndi inu bambo Mbewe, 6 July imatanthauzanji pa mbiri ya Malawi? Tsikuli ndi lokumbukira kuti dziko la Malawi lidatuluka mmanja mwa ulamuliro wa Angerezi omwe ankadziwika kuti atsamunda. Kalelo Amalawi adalibe mphamvu iliyonse pa kayendetsedwe ka dziko koma kumangotsatira zomwe azunguwo ankafuna kufikira pomwe ulamuliro wawo udagwetsedwa. Tsikuli lili ngati chikumbutso chabe koma ndi tsiku lofunika pa mbiri ya dziko la Malawi. +Kodi kalelo zimakhala bwanji pokumbukira tsiku limeneli? Sizisiyana kwenikweni ndi momwe zimakhalira masiku ano kungoti panopa zidakhala ngati zidakhwepa pangono. Kalelo, kunkakhala galimoto zonyamula ana a sukulu kupita nawo kubwalo la chikondwerero komanso lidali tsiku lolemekezeka. Pano si anthu amatha kukagwira ntchito zawo tsiku ngati limeneli? Kale kudalibe zoterezi. +Mukati tsikuli layenda bwino mumaonera chiyani? Choyambirira ndi tchuthi. Anthu samapita kuntchito ngakhale ganyu komanso mbendera ya Malawi imakhala petupetu mmalo osankhidwa. Uku kumakhala kusonyeza kuti kwachadi ku Malawi, chitsimikizo choti anthu ayera mmaso ayamba kudzilamulira. Zambiri zimachitika monga zionetsero zosiyanasiyana, mapemphero ndi masewero. Aliyense amakhala okondwa ndi wa chimwemwe. Asilikali a nkhondo nawo amakhala ndi chionetsero chawo kusangalatsa anthu ndipo mtsogoleri wa dziko amalankhula mawu a chilimbikitso ku mtundu onse. Omwe adali nkuthekera amatha kupanga maphwando mnyumba zawo. +Nanga momwe zimakhalira masiku ano mumaona bwanji? Cholinga cha tsikuli chimakwaniritsidwa? Tingaterobe poti nanga si anthu amakhala akukumbukira ufulu odzilamulira koma aaa, pena pake pamacheperabe. Kalelo kukonzekera kumayamba masiku angapo tsiku lenileni lisadafike. +Nanga inu a Malunga tiuzeni za mbiri ya tsikuli. +Tsikuli lidakhazikitsidwa pafupifupi zaka 52 zapitazo mboma la chipani chimodzi kuti anthu azikumbukira momwe adalandirira ufulu odzilamulira okha. Kunena zoona, pomwe zidafika zinthu nthawiyo mmanja mwa atsamunda, kudali kofunika kuti ufulu ngati umenewu uperekedwe. +Mukutanthauzanji pamenepo? Akuyamba kuimba ndi zaka 5 pano kudalibe. Anthu akuda eni nthaka ankakhala ndi malire mdziko mwawo momwemuno, padali malo ena omwe munthu wakhungu lakuda samaloledwa kufikako chabe chabe ndipo akamati ufulu udali mmanja mwa anthu obwera zidalidi zowona. Mabizinesi ndi ma esiteti akuluakulu adali mmanja mwa azungu ndipo anthu akuda adali a ntchito chabe. +Nanga poti ena amati kutenga ufuluwu kudasokoneza chitukuko inu mungatiuze zotani? Kumvetsa ndi kutanthauzira nkosiyana. Omwe adakhalako mu ulamuliro wa atsamunda adzakuuzani zina ndipo ena omwe akugwiritsa ntchito maphunziro potanthauzira zinthu adzakuuzani zina. Sindikuuzani maganizo anga koma ndikufusani funso lomwe Amalawi ena ofuna ayankhe pawokhapawokha. Chabwino nchiti kukhala mchitukuko chomwe sungadyerere nawo nkumalimbikira movutika wekha kuti uzisangalala? Muyankhe nokha mumtima. +Taunikirani bwino pakusiyana kwa moyo wa masiku ano odzilamulira ndi moyo wakale wa mmanja mwa atsamunda. +Moyo umakoma ndi ufulu kulikonse. Mudzaone munthu wachuma yemwe ali ndi ngongole zambiri ndi munthu osauka yemwe akudya zochepetsa zomwe alinazozo, amaoneka osangalala ndani? Ufulu ndi ufulu kulikonse palibe kuti ukukhala kapena kugona potani koma ngati uli mfulu ndiwe munthu. Kwa ine bola pano chifukwa Amalawi ali ndi malo olimapo, okhalapo komanso ali ndi mphamvu zopanga malamulo oyendetsera dziko okha umenewu ndiye timati mtendere. Inu simungakhale ndi banja nkumayembekezera kuti wina wake abwere nkumakuuzani zoti muchite ndi momwe mungayendetsere banjalo. Umu ndimo zidalili kalero. +Gule wa utse ku Nsanje Mtundu ulionse umakhala ndi zinthu zokumbikira mtundu wawo kapena chikhalidwe. Umu zilinso choncho ndi mtundu wa Asena ku Nsanje komwe kuli gule wa utse. Mbomalo mudali mwambo wobzala mitengo, ndiye gule ameneyu adamuitana kuti asangalatse anthu. Abambo adafa ndi kuseka amayi akupukusa chiuno molapitsa. BOBBY KABANGO adali komweko ndipo adamuitananso kuti avine ndi mayi mmodzi. Atatha zonse, adacheza ndi mayi mmodzi motere: Poimba amagwiritsa ntchito matabwa Dzina ndani mayi? Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ndine Fakilesi Nachikadza, ndimachokera mmudzi mwa Therere kwa T/A Malemia mboma lino. +Gule wanji wokoma chonchiyu? Ameneyu ndi utse. Utse ndi gule wa amayi okhaokha. +Atsikana saloledwa kuvina nawo? Sangakwanitse kuvina. Guleyutu amafunika munthu amene angavine kwa nthawi yaitali osatopa, ndiye atsikana sangakwanitse koma ife akuluakulu. +Mumavina nthawi iti? Timavina kukakhala zochitika monga kulonga mfumu, ndi zochitika zilizonse monga kubzala mitengoyi. +Mavinidwe ake ngotani? Limakhala gulu la amayi okhaokha, ndiye timasema timatabwa ndipo aliyense amakhala ndi matabwa awiri amene amawamenyetsa kuti zizimveka bwino. Ena amakhala akuomba mmanja ndipo onse amaimba nyimbo. Mayi mmodzi amakhala akuduka mchiuno. Iyeyu ndiye amaimirira pamene ena onse amakhala pansi. Amene akuvinayu amakhala ndi wenzulo yomwe amaimba. +Mutanthauza kuti amavina ndi munthu mmodzi? Eya, koma tingathenso kumulandira chifukwa tonse timadziwa kuvina kwake. +Amavina bwanji? Momwe ndikuchitiramu basi, nkhanitu ndi chiunochi kuchigwiritsa ntchito. Inuyonso tabwerani apa ndivine nanu kuti mukalembe zoona.eyatu ndi momwe timavinira guleyu. +Mudayamba liti kuvina guleyu? Ine ndidabadwa ndipo ndidamupeza, timaonera makolo akuvina mpaka lero takula ndipo tikuvinanso. +Nyimbo mumaimba ija mumati chiyani? Imeneyi ndi nyimbo yokamba za ubwino wa mitengo. Timati; azimayi tendene, aye! Azimaye tendene, tikabzale mitengo. Mafumu ali pomwepo, aye! Mafumu ali pomwepo tikabzale mitengo. +Pagulu ponsepa amene amavina bwino ndi inuyo? Aliyense amavina bwino koma leroli anasankha ine kuti ndivine ndipo mwaonanso abambo ambiri akuyamikira kuti ndavina bwino. n Kuikira kumbuyo khalidwe loipa Wolemba: Rabecca Nsomba Nthawi zina, amayi amene akukwatiwa amauzidwa kuti asakasiyire wa ntchito kuphika chifukwa wantchitoyo akhoza kulanda banja. Enanso nkumamulangiza kuti asakaleke kudzisamala kuopa akathawidwa. +Tikaonetsetsa palibe vuto ndi kusamala pakhomo, kudzisamalira ndi zina zotero, koma nzolakwika kuika zinthuzi ngati zida zothandizira kuti banja lisathe. +Chifukwa polankhula motere timakhala ngati tikuvomereza kuti zina mwa izi ndi zifukwa zoyenerera popangitsa kuti bambo azichita zibwenzi chifukwa mkazi wake walephera penapake. +Abambo ena amakhala ndi zofooka zina zikuluzikulu zomwe amayi amazipirira mmakomomu osaganizirakonso kuti mwina apeze mpumulo popeza chibwenzi. +Nchifukwa chiyani zimaoneka zabwinobwino kuti abambo azilephera kupirira nkufika pomasirira Naphiri kuti mpaka apange naye chibwenzi chifukwa waphika bwino? Abambo otere ngachimasomaso ndipo amakhala kuti Naphiriyo amamusirira kale. +Pali abambo ena autchisi, ena oti akavula nsapato fungo nyumba yonse. Sudzamupeza mayi akuti bola Joni okonza maluwa amadzisamalirako. Mmalo mwake mayi amayesetsa kuti akonze nsapato ndi sokosi za mwamuna wake kuti fungo lichepe. +Koma mzimayi akamveka thukuta, ndiye bambo ali ndi chifukwa chomveka bwino choti akasake chibwenzi? Osamuuza mkazi wako za vuto lake bwa? Mundimvetse, sindikuti amayi atayirire, koma tizindikire kuti amayi amakhala ndi zofooka. Tsono zofooka za amayi zisakhale zifukwa zokwanira zoti abambo azinka nasaka akazi ena. +Momwe mzimayi amapiririra zofooka za mwamuna wake, mwamunanso apirire za mkazi wake ndipo pamodzi athandizane kukonza zinthu. +Osati mmalo mokonza zinthu tizipititsa patsogolo maganizidwe olakwika omati mayi azipirira pomwe bambo akangoona vuto azikhala ngati wapatsidwa chiphaso chomachita zibwenzi. Izi ndi zolakwika. +Ma playoffs afika pena Wolemba BOBBY KABANGO G anizo lokhala ndi timu ya chi 16 mu ligi ya TNM lakhala loterera pamene nkhondo ya Dedza Young Soccer komanso Super League of Malawi (Sulom) yafika pa lekaleka. +Dedza idatenga chiletso Lachisanu pa 11 March kubwalo lalikulu la milandu mumzinda wa Lilongwe kuletsa kuti Sulom isachititse masewero ofuna kupeza timu ya nambala 16. +Chiletsocho chidaperekedwa ku Sulom Loweruka masewero oyamba pakati pa Airborne Rangers ndi Wizards atachitika kale Lachisanu. +Chiletsocho chidagwira ntchito pa masewero otsatira amene amayenera akhale pakati pa Dedza ndi Airborne Lowerukalo pabwalo la Civo. +Lowerukalo mmawa, Sulom idapita kubwalo kuti akachotse chiletsocho koma mpaka pofika Lachinayi chidali chisadachotsedwe. +Wachiwiri kwa pulezidenti wa Sulom, Daud Suleman, polankhula Lachitatu usiku adati chiletsocho chavuta kuchotsa chifukwa jaji wake adachoka. +Tidauzidwa kuti jaji wapita ku Zambia, ndiye panopa tikumva kuti jaji wina ndiye athandizire kuti chiletsocho chichoke kuti masewero ofuna kupeza timu ya nambala 16 apitirire, adatero Suleman. +Timu ya Dedza ikuti ngati Sulom ikufuna kupeza timu ya nambala 16, akuyenera atenge iwo chifukwa ndiwo adathera pa nambala 13 kutsatirana ndi Wizards komanso Airborne. +Koma Suleman akuti njira yosewera ma playoffs ndi yokhayo yomwe Sulom idagwirizana kuti ichitike pofuna kupeza timu imodzi yoonjezera. +Ligiyi tsopano kuyambira chaka chino izikhala ndi matimu 16 osati 15 monga zakhala zikuchitikira koma bungwe la Sulom lidalengeza ganizo lochita ma playoffs patadutsa pafupifupi mwezi chithereni ligiyi. +Ngati chiletsocho chichotsedwe, ndiye kuti Sulom ikuyembekezereka kulengeza tsiku lomwe ma playoffs-wa achitike. +Mwini wake wa Wizards Peter Mponda akuti izi zawasokoneza kwambiri. Taononga ndalama zambiri, mayendedwe, chakudya komanso malo ogona ndi ndalama zambiri zimenezo, adatero Mponda. +Wizards ndiyo idapambana mmasewero ake ndi Airborne 2-1. +Kuthamanga kwa magazi nkopeweka Kuthamanga kwa magazi ndi amodzi mwa matenda omwe amatenga miyoyo ya anthu mwadzidzidzi. Kwa nthawi yaitali anthu akhala akuganiza kuti matendawa amagwira anthu olemera okhaokha, anamadya bwino komanso onenepa. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Koma malingana ndi kufotokoza kwa dotolo wa nthendayi kuchipatala cha Kamuzu Central mumzinda wa Lilongwe, a Dr Lumbani Munthali, matendawa akhoza kugwira munthu aliyense ngakhale kuti onenepa ndiwo amakhala ndi pachiopsezo chokulirapo kudwala nthendayi. +Kusuta fodya kukhoza kudzetsa nthenda ya kuthamanga kwa magazi A Munthali adati: Nthenda ya kuthamanga kwa magazi imayamba kaamba ka zifukwa zosiyanasiyana. Thupi lili ndi mitsempha yomwe magazi amadutsamo kotero mitsemphayi ikaphinjika ndi kuchepa, zimachititsa kuti magazi ayambe kuyenda mothamanga. +A Munthali adati ngakhale anthu amene amadwala nthendayi popanda chifukwa chenicheni, anthu ambiri amagwidwa ndi nthendayi kaamba kosuta fodya, kumwa mowa, kuyamwira ku mtundu, kusachita majowajowa, kudya zakudya zamafuta komanso za mchere wambiri. +Mitsempha ya munthu amene sachita masewera olimbitsa thupi siyitakasuka moti magazi amathamanga kwambiri. Anthu ena amadwala nthendayi ngati ku mtundu kwawo wina anadwalapo nthenda ngati yomweyi. Masiku ano anthu ambiri akukhala moyo wapamwamba ndipo zakudya zawo ndi zamafuta kwambiri komanso anthuwo nthawi zambiri amayenda chokhala ndipo sagwira ntchito zolemetsa. Izi zikuchititsa kuti azikhala pachiopsezo chachikulu chogwidwa ndi nthendayi, adatero a Munthali. +Mmodzi mwa anthu omwe akudwala nthendayi ndipo amalandira thandizo la mankhwala pachipatala cha Kamuzu Central, a Felix Gondwe, adati amakhulupirira kuti thendayi idawagwira mchaka cha 1981 kaamba koti adalekerera thupi lawo ndipo sankachita majowajowa. +Ndidalibe galimoto koma nthawi zonse ndinkakwera nawo galimoto ya mnzanga. Sindinkachita majowajowa alionse kuti ndilimbitse thupi langa. Ndidanenepa kwambiri ndipo mchaka cha 1981 ndidapezeka ndi nthenda ya kuthamanga magazi,adatero a Gondwe womwe amakhala ku Area 36 mu mzinda wa Lilongwe. +Ngakhale kuti nthendayi ilibe zizindikiro zikuluzikulu, a Munthali adati munthu yemwe ali ndi nthendayi amamva kupweteka kwa mutu, chizungulire, kuthamanga kwa mtima, komanso saona bwinobwino. +Wotsatsa msuweni wake Amangidwa miyezi iwiri Ngati bodza, koma apolisi mboma la Nkhotakota atsimikiza kuti bwalo la milandu la majisitireti lagamula kuti Bakali Chirwa, wa zaka 37, akagwire ukaidi wa miyezi iwiri kaamba kotsatsa msuweni wake, Hussein Banda, wa zaka 22, kwa msodzi wina wake pamtengo wa K550 000. Evance Green wa zaka 50. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mneneri wa polisi mbomali, Williams Kaponda, wauza Msangulutso kuti Chirwa, wa mmudzi mwa Mkumbira, kwa T/A Malengachanzi adatsatsa msuweni wakeyo kwa Evance Green, wa zaka 50, wochokera mmudzi mwa Chilezi kwa Malengachanzi komweko, pa 8 February 2016, koma poyamba wotsatsidwayo ankaona ngati nthabwala. +Green adatiuza kuti poyamba ankawona ngati akusereula chabe koma akuti adadodoma kuti patapita masiku atatu wotsatsayo adamupezanso nkumuuza kuti amafuna ndalama mwachangu ndipo amafunitsitsa bizinesiyo itayenda mwachangu, adatero Kaponda. +Akadagulitsidwa: Banda Iye adati wotsatsidwayo adangouza mwini malondayo kuti amuyankhabe ndipo atasiyana adakanena kwa a nyakwawa Chilezi yemwe adamuuza kuti amuuze poti angakumane kuti malonda achitike, osadziwa kuti adamukonzera kampeni. +Kaponda adati tsiku lokumanalo, nyakwawa Chilezi adaitanitsa mboni mwachinsinsi kuti zidzamve zokha mwamseri za malonda achilendowo ndipo zina mwambonizo adali makolo awo a wotsatsa ndi wofuna kugulitsidwayo. +Mudavuta mukhothi, Lachisanu lapitali [pa 11 March] woimbidwa mlandu ataona kuti pakati pa mboni padali makolo ake, ndipo adanenetsa kuti adamvadi momwe zokambirana za bizinesiyo zidayendera, adatero Kaponda. +Wofufuza nkhani za polisi mbomalo, Francis Banda, adati awiriwo atakambirana kwa kanthawi adagwirizana kuti agulitsane munthuyo pamtengo wa K500 000 ndipo kuti ayamba kupatsana theka kuti theka linalo adzapatsane popatsana malondawo. +Iye adati pofuna kuti wotsatsa malondayo asadzakane pamawa kuti walandira ndalama, adagwirizana kuti aitane mboni zoonerera akamapatsana ndalama zoyambirazo ndipo Chirwa adadzidzimuka kuona kuti mbonizo padali mayi a wogulitsidwayo ndi mchimwene wake (wa Chirwayo). +Adangoti kakasi ndipo ife tidatsegula mlandu pomwepo mpaka adakalowa mukhothi momwe adalephera kuukana mlandu ndipo woweruza First Grade Magistrate Juma Chilowetsa adamupatsa miyezi iwiri kuti akagwire ntchito yakalavulagaga pa mlandu wochita zomwe zingasokoneze mtendere, zomwe ndi zotsutsana ndi gawo 168 ya malamulo, adatero Banda. +Green adauza Msangulutso lachinayi lapitali palamya kuti adali wodabwa ndi wamantha kumva munthu akumutsatsa malonda a munthu chonsecho sadamvekepo mbiri yochita malonda kapena masiramusi a ziwalo za anthu ndipo ichi ndicho chidamuchititsa kukadziwitsa a mfumu nkhaniyo isadafike pena. +Ankatsatsa msuweni wake: Chirwa Tidakumana ndi kuchokera kunyanja ndipo adandilonjera nkundiuza kuti adali ndi mawu. Nditampatsa mpata wolankhula adandiuza kuti adali ndi malonda koma malonda ake adali munthu. Ndidangoseka poona ngati macheza chabe, adatero Green. +Iye adati kenako awiriwo adayamba kutsogozana mpaka pakhomo pake kenako wotsatsa munthuyo adatsanzika. +Tsiku lina adadzandipeza pakhomo ndipo ndidamulonjera koma ndidadzidzimuka kumva kuti wabweranso ndi nkhani yomweyo ndiye ndidachita mantha kuti mwina kapena anthu akundiganizira zolakwika ndiye ndidakanena kwa a mfumu, iye adatero. +Mkuluyu adati mfumu sidazengereze koma kumuuza kuti aoneke ngati akufunadi malondawo ncholinga choti amukole wotsatsa munthuyo kuti nkhani ikapita kupolisi ikakhale ndi umboni ndipo zidachitikadi monga momwe mfumuyo idanenera. +Green adati wakhala akuchita usodzi kwa nthawi yaitali osagwiritsa ntchito chizimba chilichonse ndipo zimamuyendera bwinobwino komanso ali ndi makasitomala ambiri omwe amachita nawo bizinesi. +Mwina amangoona momwe zimandiyendera nkumaganiza kuti ndi mankhwala pomwe ayi ndithu, ndimachita chilichonse mchilungamo ndi choonadi basi, adatero mkuluyu. +Tidakanika kuyankhula ndi Banda, mnyamata amene adali pamalonda, kaamba koti tidalephera kupeza nambala ya foni yake. +Potsirapo ndemanga pachigamulochi ndi chilango chake, katswiri wa zamalamulo kusukulu yaukachenjede ya Chancellor College, Edge Kanyongolo, wati olakwa ndi omwe adatsegula mlanduwo chifukwa kutsatsa munthu si mlandu waungono ngati momwe adauonera. +Iye adati oweruza milandu amagamula potengera zomwe auzidwa mukhothi, osati momwe ntchimolo lilili chifukwa amagwiritsa ntchito zomwe malamulo amanena. +Wogamula mlandu amangomva zomwe ozenga ndi ozengedwa akunena nkupanga chigamulo, ndiye ngati ozenga apereka mlandu wopepuka chigamuloso chimapepukanso. Apa ozenga mlandu akadapereka mlandu waukulu kuti wogamula naye apereke chilango chachikulu, adatero Kanyongolo. +Naye womenyera ufulu wa anthu, Timothy Mtambo, adati nzokhumudwitsa kuti anthu omwe amapezeka ndi milandu yoopsa amalandira zilango zopepuka, zomwe zimawapatsa danga lokabwereza mlanduwo. +Iye adati malamulo ambiri adapangidwa kalekale ndipo ndi ofunika kuunikidwanso kuti zilango zake zizifanana ndi chomwe walakwacho kuti azitengerapo phunziro, komanso anthu ena omwe adali ndi cholinga chopanga zomwezo asamapangire dala. +Mmera watuluka koma samalani, atero katswiri Mmera watuluka ndipo momwe zikuonekera alimi ambiri akhoza kuchita mphumi chaka chino zinthu zikapanda kusintha, makamaka pakagwedwe ka mvula. Koma katswiri wa zamalimidwe wati mvula ili apo, mpofunikanso kutsatira njira zoyenera paulimi. +Mkulu woyanganira za ulangizi ndi njira zamakono zamalimidwe, Dr Wilfred Lipita, wati mmene mvula yayambira ndi mwayi wa alimi kutsata njira zoti asadzakumane ndi zomwe zidaoneka chaka chatha. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Poyankhula ndi Uchikumbe, mkuluyu adati, mwa zina, ino ndiye nthawi yabwino yoti alimi akhoza kukolola ndi kusunga madzi ambiri kuti kutabwera ngamba mwadzidzidzi asadzanongoneze bondo mmera wawo omwe watuluka kale bwinowu ukufota. +Tiyeni tichilimike panopa pomwe mvula ikugwamu. Tiyeni tikolole madzi ambiri kudzera mnjira zosiyanasiyana zomwe timadziwa zija nkusunga madzi ambiri chifukwa njira yokolola madzi ndi imodzi mwa njira zodalirika tsopano, adatero Lipita. +Iye adati alimi asalole udzu kapena zitsamba kutasa mminda chifukwa zimaononga chakudya cha mbewu mmalo moti mbewu zidye chakudya chokwanira ndi kukula msanga mothamangitsana ndi mvula. +Mvula ndi yosadalirika iyi masiku ano moti ikamagwa chonchi ndi nthawi yoti alimi tiigwiritse ntchito osalola kuti mwayi utiphonye. Mmunda mukangooneka udzu kapena zitsamba, lowamoni msangamsanga nkupalira kuti chakudya chomwe chili mnthaka chikhale cha mbewu zanu zokha, adatero Lipita. +Mkuluyu adatinso pomwe pali mwayi wa manyowa kapena feteleza, alimi asazengereze kuthira koma motsatira malangizo ochokera kwa alangizi komanso momwe unduna wa zamalimidwe umanenera. +Nthawi zambiri mvula ikachuluka, mizere ndi mbewu zimakokoloka kaamba kosowa chitetezo monga chimzere chotchinga mmbalimmbali mwa munda, milaga ndi kukwezera mizere msanga. +Mukaona kuti madzi akuchuluka mmunda dziwani kuti nthawi iliyonse mizere ndi mbewu zanu zikhoza kukokoloka ndiye njira yabwino nkuunda chimzere chachikulu mmphepete mwa mundawo, kuika milaga kapena kukwezera mizereyo msanga madzi asadachuluke mphamvu. +Malangizo a mtundu uwu amaperekedwa mwaulere ndipo ngati anthu akuona kuti pali vuto lililonse mmunda mwawo, kudera kwawoko kuli alangizi a zamalimidwe omwe ndi okonzeka kuwathandiza nthawi iliyonse, adatero Lipita. +Mu Uchikumbe wathu sabata yatha, katswiriyu adalangiza alimi kuti abzale mbewu zocha msanga komanso zopirira ku ngamba ndipo sabata ino wawonjezerapo kuti mmapando momwe mbeu zidakanika kumera ndi mofunika kupakizamo msanga. +Iye adati kupakiza msanga kumathandiza kuti mbewu zisasiyane kwambiri mmunda kuti zizilandira dzuwa ndi kuwala kofanana kuopa kuti zina zingatchingike ndi zinzake kaamba kochedwa kumera. +Ndikhulupirira pano alimi amadziwa kuti kupatula mchere wa mnthaka ndi madzi, mbewu zimafunanso dzuwa ndi kuwala kuti zizibiriwira bwino. Mbewu zokulira pamthunzi zimakhala zonyozoloka ndi zachikasu ndiye pachifukwachi, sipafunika kuti mbewuzo zizisiyana makulidwe ake, adatero katswiriyu. +Othawa nkhondo akutuwa ndi njala Kwathina kukampu ya anthu othawa nkhondo mdziko la Mozambique amene akukhala ku Mwanza ndi Neno komwe anthuwa akutuwa ndi njala. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ena atha sabata ziwiri tsopano popanda chakudya ndipo amene ali bwino ndi anthu amene adabwera ndi ndalama kuchokera mdziko lawo. +Gulupu Ngwenyama wa mboma la Mwanza wati anthuwa akusowa mtengo wogwira kupatula anthu amene adayenda ndi ndalama kuchokera mdziko lawo. +Ndiwo ndi vuto lalikulu kwa othawa nkhondo Amene adabwera ndi ndalama ndiwo sakulira kwambiri chifukwa akumagula zakudya, koma amene adangobwera opanda kanthu ndi amene akuvutika chifukwa akungodikira thandizo la mabungwe, adatero. +Gulu la anthu lidayamba kukhamukira mdziko muno kuchokera ku Mozambique komwe akugwebana pachiweniweni pakati pa otsutsa boma ndi aboma. +Kumenyanako, komwe kudayamba chaka cha tha, kudafika poipitsitsa mu January pamene nzika zina za dzikolo zidayamba kuthawira mdziko la Malawi. +Kampu ya Luwani ku Neno yomwe ikusunga anthu pafupifupi 1 400 njomwenso yakhudzidwa kwambiri ndi njalayi. Kampu ina ndi ya Kapise mboma la Mwanza komwe kuli anthu pafupifupi 900. +Malinga ndi Ngwenyama, pali chiyembekezo kuti Lolemba likudzali bungwe la World Food Programme (WPF) ligawa chakudya kwa anthuwa. +Naye Senior Chief Saimoni wa mboma la Neno wati mavuto a njala ndi osakambika chifukwa nthawi zonse kukumakhala mavuto. +Zovula pa Wenela ayi, tamva! Tsikulo pa Wenela padali ziii! Moti ojiya, osolola ndi osenza onse adali khumakhuma. Ndalamatu ndalama zalowa ku silent ndiye anthu sakuyenda. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Basi ya Lilongwe imatenga tsiku lonse kuti idzadze. Ambirinso amachita kunenera. Nchifukwa chake ndidangoganiza zolowera malo aja timakonda pa Wenela. Ndidakapeza Abiti Patuma ndi Gervazzio akumvera nyimbo ya Lucius. +Poti sitima, imaphweka akamayendetsa wina. +Sindikudziwa kuti nyimboyo adayiika chifukwa chiyani! Abiti Patuma adali bize pafoni yake. +rt Koma abale, phungu uyunso ndiye amangokhalira pa Facebook. Taonani lero akuti iye sakufuna kukwezeredwa ndalama. Ndidakuuzani kale kuti uyu wokonda kuvina kanindoyu amangofuna kuti anthu azimumvera. +Mwaiwala zija ankanena zolodza azungu osakaza la Mulanje phiri; mwamuiwala kuti ngwa nthabwala basi? adatero Abiti Patuma. +Zoona. Amati avula, ayende tauni ya Lilongwe onse aone kuti iye ndi munthu wamkulu, wotamba masana likuswa mtengo! Chomwe ndikudabwa nchakuti kodi bwanji phunguyu amachita zosiyana ndi aphungu ena? Akamabwera ku Nyumba ya Malamulo amakwera Bajaj, inde galimoto kaya ndi njinga ya matheyala atatu? Saona anzake akayenda pa galimoto zopuma ngati olemekezeka? Uyutu uyu kupanda kusamala naye adzalaula ndi pa Wenela pano! Adayankhira Gervazzio: Ndikuona ngati nzeru zikumuchepera ameneyu, mwina zamuchulukira kwambiri? Abale anzanga, kunena zoona wamisala adaonadi nkhondo! Posakhalitsa tindangoona uyo watulukira atavala mwado wofiira wopanda lisani. Kumtundaku malayanso ofiira koma odula mikono. Tsinya lili gaa pankhope. Kenaka adayambitsa nyimbo, amvekere: Zivute, zitani ife Amalawi! Chigulu chidali chitasonkhana kuti chione munthu adalonjeza kuti avula uja, chidayankhira: Tili pambuyo pa maalubinoo! Kenaka tidamva ali Left! Right! Left! Right Wayambika wa ndawala! Kuguba ulendo wa ku Nyumba ya Malamulo. +Konzani mavuto a kayidi, litero khoti Khoti la First Grade Magistrate mboma la Dowa, lalangiza boma kuti likonze ena mwa mavuto omwe akayidi akukumana nawo mndende za mdziko muno. +Mavutowa ndi monga kuthinana kosayenera mzipinda zogona, kuchepa kwa chakudya, komanso kuchedwa kutumiza kwawo akayidi ochokera maiko ena omwe atsiriza kugwira chilango chawo mdziko muno. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mkalata yomwe alembera boma kudzera kubungwe lake loyanganira ndende mdziko muno la Prison Inspectorate Committee, bwaloli lati akaidi omwe ali mndende za mdziko muno akuvutika kwambiri maka kaamba kakusalabadira kwa akuluakulu woyanganira ndendezi. +Mneneri wa boma yemwenso ndi nduna yofalitsa nkhani Jappie Mhango, akana kutsirira ndemanga pankhaniyo. Iwo akankhira kwa nduna ya za chilungamo Samuel Tembenu. Omwe nawonso akana kuti nkhaniyo sikukhudza unduna wawo koma wa za mdziko, komwe kuli Jean Kalirani. +Koma Kalilani, sitidathe kuyankhula nawo, kaamba kakuti panthawi yomwe timalemba nkhaniyo nkuti iwo ali kunja kwa dziko lino. +Kalatayo yomwe idalembedwa pa 28 August, 2015, ndipo amene adasayina ndi majisitileti Amurani Phiri, imodzi mwanjira yodalilika yochepetsera mavutowa ndi kulimbikitsa chilango chogwirira kuchokera kunyumba kwa akayidi omwe apalamula milandu yochepa. Bwaloli lati pakali pano ndende ya Maula mumzinda wa Lilongwe, ndi yomwe yanyanya kukhala ndi akayidi ambiri zedi. +Ndidakayendera ndende ya maula pa 27/08/2015, patsikuli ndidakapeza akaidi 2 532. Kuphatikizapo akaidi ochokera kunja kwa dziko lino okwana 569, omwe mwa iwowa, 230 ndi nzika za dziko la Ethiopia. +Ndipo ambiri adali atatsiriza kale kugwira ukayidi wawo, koma ankadikira kuti boma lipeze ndalama zowatumizira kwawo. Ndipo pankhani ya chakudya, ndendeyo imagwiritsa ntchito matumba 32, a ufa wa mgaiwa kudzanso matumba 8 kapena 9 a nyemba patsiku, adatero iye. +Mneneri wa Malawi Prison Service (MPS) Smart Maliro, pambali polonjeza kwa masiku angapo kuti atero, sadayankhe mafunso omwe tidamutumizira. +Ndipo poyankhapo pa nkhaniyo, mneneli wa ku nthambi yoona za anthu olowa ndi kutuka mdziko, Joseph Chauwa, wati nzoonadi kuti mwezi wa August chaka chatha, kundendeyo kudali nzika za maiko ena, maka za ku Ethiopia zokwana 400. +Koma Chauwa adati ndi thandizo la ndalama zochokera ku bungwe la International Organization for Migration (IOM), nzikazo zidatumizidwa kwawo ndi matikiti a ndege omwe bungwelo lidagula, nzikazo zidapita kwawo. +Chipatala chiutsa mapiri pachigwa Akuluakulu ena a khonsolo ya Lilongwe ndi kontilakitala yemwe akumamanga chipatala cha Biwi mumzinda wa Lilongwe, ayankha mafunso zitadziwika kuti pantchitoyi pakukhala ngati padayenda zachinyengo. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Nduna ya maboma angonoangono Kondwani Nankhumwa wanenetsa kuti ena anjatidwa pankhaniyi kafukufuku akatha. +Chomwe chautsa mapiri pachigwa nchakuti chipatalacho chayamba kale kugwa mbali imodzi chisadathe komanso makoma ali mingalu yokhayokha. +Nankhumwa (Kumanzere) sadakhulupirire kuona mmene ntchito ya Chipatala cha Biwi ikuyendera Nankhumwa adanenetsa kuti pantchitoyi, yomwe ndi ndalama zokwana K198 miliyoni, padayenda chinyengo chachikulu chomwe iye akuti ndi Kashigeti ndipo wati ofufuza akamaliza, onse okhudzidwa adzayankha mlandu wosakaza ndalama za boma. +Polojekiti yaikulu ngati imeneyi idayamba bwanji popanda pulani iliyonse? Chimenechi ndiye chinyengo choyambirira. Chachiwiri, zidatheka bwanji kumusiya kontilakitala kuyamba kumanga mpaka kufika pokhoma malata osazindikira kuti akupanga chinyengo? adatero Nankhumwa akuthambitsa akuluakulu a khonsolo ya Lilongwe ndi mafunso Lolemba lapitali. +Panthawiyi ndunayi idakayendera chipatalachi itamva kuti chagwa mbali imodzi ndipo mkati monse ndi mingalu yokhayokha komanso zitseko ndi zimbudzi zidaphotchokaphotchoka ngakhale kuti chipatalacho sichidathe. +Iye adati unduna wake sulekera pomwepa koma ufufuza momwe kontilakitalayo adapatsidwira ntchitoyo ndi zonse zomwe zakhala zikuchitika pachipatalapo ndipo pakapezeka zachinyengo chilichonse, onse okhudzidwa adzazengedwa mlandu. +Tikukamba apazi ndi ndalama zambiri zedi ndipo nzodabwitsa kuti nthawi yonseyi kontilakitala amagwira ntchito yosaoneka bwino ngati iyi akhonsolo adali kuti? Ichi nchinyengo chachikulu ndipo tifufuza mpaka ena azengedwapo mlandu apa, adatero Nankhumwa. +Ndalama zomangira chipatalachi zidachokera kudziko la Japan ndipo Nankhumwa adati ndi momwe zakhaliramu, boma silikudziwa koti lingatenge ndalama zokonzeranso chipatalachi kuti chilongosoke. +Mkulu wa khonsolo ya Lilongwe, Moza Zeleza, adavomereza kuti ntchito yomanga chipatalayo sidayendedi bwino ndipo kuti kontilakitala sadagwire nthawi yomwe amayenera kumaliza ntchitoyo. +Iye adavomereza kuti ntchitoyo idagwiridwa mwa mgwazo, kontilakitala adagwiritsa ntchito zipangizo zosayenera, adaphonya nthawi komanso khonsolo idalephera pantchito yoyanganira kumangidwa kwa chipatalacho. +Ntchitoyi sidayendedi bwino, ayi, moti tidakamangala kale kubungwe la a zomangamanga la Malawi Institute of Engineers (MIE) omwe adatipatsa chilolezo cholemba katswiri woti aunike bwinobwino chipatalachi ndi kutiuza choyenera kuchita, adatero Zeleza. +Iye adati khonsoloyi singachitire mwina koma kudikira zomwe adzanene katswiriyo ngakhale kugwetsa chipatala chonsecho nkuyambiranso chifukwa momwe chilili, nchiwopsezo chachikulu kumiyoyo ya anthu. +Zeleza adati chipatalachi chikadayenda bwino nkutha, chikadachepetsa chiwerengero cha amayi a mmadera asanu ndi awiri (7) omwe amayenda mtunda akafuna thandizo la chipatala. +Ena mwa madera omwe akadapindula nawo chipatalachi chikadatha ndi Biwiyo, Area 36, Area 24, Area 22, Chipasula ndi Kaliyeka, madera omwenso kumachokera anthu ambiri mumzindawu. +Kupatula chipatala cha Kawale, chipatala china chomwe anthu a mmadera asanu ndi awiriwa amadalira ndi cha Bwaila ndipo nchokhacho chomwe amayi oyembekezera a mmaderawa amakachilirako. Chiptala chomwe tikukamba panochi [Biwi], chidakakhalanso ndi malo ochilirako amayi, kutanthauza kuti mavuto ena monga othithikana ku Bwaila akadachepa, adatero Zeleza. +Mneneri wa unduna wa maboma angonoangono Muhlabase Mughogho adati undunawu utakayendera chipatalachi koyamba chaka chatha udapeza kuti pansi ndi makoma mudali mingalu yochititsa mantha. +Iye adati atatsina khutu akhonsolo, adapitako ndipo adakapeza ogwira ntchitoyo akutchinga mingaluyo ndi matayilosi komabe sizidathandize chifukwa matayilosi ena amapotoka pomata. +One-man demo pa Wenela tsikulo pa wenela padaterera. zidaliko. nkhani idavuta ndi ija tidaiyamba sabata yatha. Inde, iyi nkhani yophana chisawawa, makamaka kwa abale athu achialubino. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Izi zikumvekazi zidandikumbutsa zomwe ndidamvapo mmbuyomu kuti Manyasa kalelo ankaponyera kuphompho odwala khate, kuja ku Zomba. Mitembo yawo inkapezeka mumtsinje wa Namitambo. Koma nanga lero zoona kuphanaku zatani? Abiti Patuma adali pafoni ndipo amangodzuma. Uku tidali tikuonera kanema. +Zoona pa CNN, BBC, Al Jazeera ndi ena onse akunja akufalitsa za nkhanza tikuchitirana tokhatokhazi! Kodi izi ndiye azungu abweranso kuno kwathu kudzatisiyira enafe ma dollars, ma rands ndi zina zotero? adafunsa. +Zonsezi ndi Moya Pete ndi anzake. Izitu sizikadafika apa akadalimbana nazo koyambirira komwe kuja. Nkhani zikangokhudza United Nations komanso Amnesty International umangodziwiratu! Mwaiwala adathana ndi gogo uja ndani? adatero Gervazzio. +Zoona, ndikumbuka masiku amenewo ndili kwathu kwa Kanduku, tinkamva kuti bungwe la Amnesty International lidalimbikitsa kuti zinthu kuno zisinthe makamakanso chifukwa cha kumangidwa kwa andale ena popanda chifukwa komanso kuphedwa kumene. +Mwaiwalanso muja UN idavutira nthawi ya Mfumu Mose? Zoti munthu ngwamakani kuiwaliratu, adatero Abiti Patuma. +Chomwe ndikudabwa ine nchakuti dziko lino lidaliko kuyambira kale koma izi zachuluka chomwechi nthawi ya Moya Pete, bwanji? ndidafunsa. +Palibe adandiyankha. Adangoti duuu! Posakhalitsa adatulukira mkulu wina ali chibadwire. Iyetu adanyamula chikwangwani cholemba kuti Osapha! Tonse tidayangana kumbali. +Abiti Patuma adathawira kukauntala, adatenga chikwama chake pomwe amasungitsapo nkusololamo chovala chamkati chofiira. +Chonde, atate, amamangatu izi zoyenda bunobunozi. Amene samangidwa ngwamisala basi. Tavalani basi, tilibetu ndalama zogulira nthochi kuti tizikakuonani akakunjatani, adatero Abiti Patuma. +Kaya mkulu uyu ndidamuonapo kuti kaya? Koma nkhope yake ndi yosasowa. +Ndipo tangoganizani kuyenda malipsata mukuchitako, Paparazzi akatola zithunzi nkuika munyuzi, mwana wanu nkuona, ulemu wanu ukhalaponso? adatero Gervazzio. +Nkhope yakeyo si yosowa, koma kaya ndidamuona kuti mkulu ameneyu? Kodi ndi uja adali ndi bwenzi lonenepa zedi ankalimbirana ndi mnyamata wa magitala uja? Tonse takwiya, koma chonde ife zomationetsa filimu zolaula masanasana takana. Akapanda kukutenga apolisi tiitanitsa a Censorship Board, adatero Abiti Patuma. +Mwamaliza? Ndakwiyatu kwambiri. Ndine legistrator, ntchito yanga ndi yopanga malamulo. Apapatu aphungu komanso boma timayenera kubweretsa Group Areas Act chifukwa nkhaniyi ikuposa nkhani ya njala, adatero mkulu uja, thovu likukha. +Dekhani, achimwene. Anzanu enatu adayamba ndi matukutuku chomwechi koma adakathera kuti atapezeka kuti satifiketi ya 8 adalibe? adafunsa Abiti Patuma. +Kaya mkulu ameneyu ndidamuonapo kuti? Koma atavala bulauzi ndi phwanyamchenga zingamukhale bwanji! Kaya mundipha, kaya mundidya, ine ndivula basi, adafuna kuchotsa kabudula wamkati adapatsidwa ndi Abiti Patuma uja. +Mulibe Sisters ali kuti? Tikamalira, muzitimvera Tikamalira, musamakwiye Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mudziwe ndife ana anu Sindikudziwa kuti nyimbo ya Lucius Banda idabwera bwanji mmutu mwanga. Ndipo sindikudziwa chifukwa chimene nyimboyo idayalira mphasa mmutu mwangamo. +Mwinatu malingaliro adali pazochitika mu 2012 pomwe nyimbo ya Achoke! Achoke! idali pakamwa pamavenda ambiri. Nthawiyo nkuti anyamata ena otchedwa Paki atauza Mfumu Mose kuti apakire zake pasanathe miyezi iwiri. Miyezi iwiri isanati kutha, Mfumu Mose nkuti itapita kumadzi kukazula chinangwa. Ndipo inali isanatiuze ngati anyamata aja apachibale Mustafa ndi Ajibu angalandirane mpando wonona pano pa Wenela. +Anyamatatu a Paki si pano. Ndikumbuka adamufumbatitsa mpweya gogo uja adandipeza nditavula shati pomwe ndinkalima kwathu kwa Kanduku ndipo adalowera uku ndi uko kunena kuti adatipeza tili chinochino. +Abale anzanga, Paki si pano! Paki palibenso. +Koma kodi amvanako kuti chiyani? Kodi anenapo chiyani pazakupezeka kwa chakudya? Tileka liti kugona mmisika ya Admarc? adafunsa Abiti Patuma. +Bambo amene adali naye adamudula. +Akuluakulu, inetu ndili mmadzi. Dzulo ndinatenga msungwana wina mgalimoto yanga. Sindimamudziwa koma panjira adakomoka. Ndidapita naye kuchipatala. Atakhala nthawi pangono dotolo adati wasangalala kuti mkazi wangayo wabala mwana. +Ndidamuuza dotoloyo kuti si mkazi wanga. Koma atamufunsa mkaziyo, adanenetsa kuti ndine mwamuna wake. Ndidati tiyezetse ngati mwanayo adalidi wanga. Atandiyeza dotolo adati sizingatheke kuti ndikhale bambo chifukwa ndidagwa mumtengo wapapaya. Chomwe chidandiliza nchakuti mkazi wanga ali ndi ana anayi. Tsono bambo wa anawo ngati si ine ndi ndani? adamaliza mkuluyo. +Ndidafuna kuseka. Ndidafunanso kulira nthawi yomweyo. +Tidaona anthu akulimbana pa Wenela. Tidakhamukira kumeneko. Tidaona kamnyamata kena kakugawa chimanga. Onse ankangoti Major! Ine amvekere Go higher man of God! Mnyamatayo adali kugawa chimanga. +Ndithu this is miracle maize. Mukakagayitsa chimangachi, ndithu dengu lanu silidzatsikanso. Miracle maize! Zikuonekatu zija adaona mayi uja adasunga Elisha masiku adzana, adatero mnyamata uja. +Inetu paja zoweruza ayi. +Mkazi wa mnyamata uja, Meliya, adaima: Ndikuchitira umboni ine. Mayi wina adabzala mbuto kumpingo wathu wounikirawu. Adapita kubanki kukatenga ngongole imene adagulira galimoto. Koma kuti ayambe kubweza ngongole, abanki adati mapepala ake asowa. Go higher! Shout a better Amen! Ndiyo nkhani tidabwerera nayo pa Wenela. +Kodi Moya Pete amene akuoneka kuti zikumulakayu sakadamupeza mnyamatayu kuti chimangachi akuchipeza kuti? Ndithu akadakapezako mmalo momangonena kuti chiliko kumsika. +Sangayerekeze, adatero Abiti Patuma. Akadakhala wanzeru akadapita kukagwada kwa Mulibe Sisters kunena kuti amukhululukire. Mwaiwala kale kuti Mfumu Moya isanapite kumtsinje kukazula chinangwa ndipo njala idasautsa pano pa Wenela, tidapulumukira chimanga cha Mulibe Sisters amene adachibweretsa pano pa Wenela, ku Ndirande, Chirimba, Chilomoni, Bangwe, Ndirande ndi madera ena? adatero Abiti Patuma. +Palibe icho ndidatolapo. +Dizilo Petulo Palibe, polisi Nthawi imeneyo nkuti tikudikira Moya Pete kuti atiuze njala athana nayo bwanji pano pa Wenela. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Tonse tidaungana poawailesi kuti timve kuti izi zomagona kumsika wa chimanga nkungololedwa kugula makilogalamu 10 okha zitha liti. Pajatu Dizilo Petulo Palibe mogwirizana ndi Moya Pete adatiuziratu kuti iwo ndi akadaulo pothana ndi njala. +Aliyensetu amadziwa kuti awa ndi akatakwe pothana ndi njala. +Chodabwitsa, 1 koloko yomwe amati atilankhulayo idakwana nkudutsa. 2 koloko idakwana nkudutsa, kuli ziii! Abiti Patuma adamuimbira mnyamata wodziwa kuika phanzi mkamwa mwake, Geri Waola. +Kodi zikukhala bwanji? Kumphikako 1 koloko imakwana cha mma 4? Tikudikira kumva Moya Pete ife, adatero Abiti Patuma. +Waola adamuyankha kuti adati 1 koloko idali nthawi yakuti atape mawu a Moya Pete. +Usiku watsikulo, Moya Pete adatipeza pa Wenela. +Ndithu ndawalambwaza asilikali kuti azigwira akuba chimanga, adayamba. +Mukuchita kuwauza chochita? Simesa ndi ntchito yawo? Timayesatu mutiuza kuti mwatipezera chimanga uku ndi uko kuti kungwemphaku kukhoza kutha, adatero Abiti Patuma. +Sadayankhe Moya Pete. +Nanga zinakhala bwanji? Ndimayesa anati mutilankhula tonse 1 koloko? adaponya funso lina. +Sanamvetse ndi waola ndi anzake. Ine ndinawauza kuti ayambe kundijambula 1 koloko koma iwo anafalitsa kuti ndinawauza kuti ndikulankhulani nonse okhala pa Wenela nthawi imeneyo. Kaya nkuwatani anthu amenewa kaya, adatero Moya Pete. +Abiti Patuma adalandira foni. Adalankhula pangono nkudula. +Kenako adati: Tade, tiyeko ku Machinjiri. Mkulu wina akundikodola, adatero. +Tidalowera komweko. Koma moto umene tidaupeza uko! Kudali kuotcha khoti! Kuotcha bwalo la milandu. +Anthu akuotchawa si mbanda zimenezi zikufuna milandu yawo isokonekere? ndidafunsa. +Kaya. Komai ne ndikuonanso ngati ndi anthu a njala awa. Kutopa akungofuna kupeza pophwetsera, adandiyankha Abiti Patuma. +Posakhalitsa, chidafika chimbaula. Chidaponya utsi wokhetsa msozi. Pafupi ndi khotilo pali chipatala chachingono, kumenenso amayi oyembekezera amachilira. +Ndidaona mayi wina wooneka wotopa akutuluka kuthawa mchipatalamo. Mayi winanso amene akuoneka kuti adali atangobereka kumene adatulukanso mchipatalamo, khanda lake lili kumanja. Misozi ili kamukamu. Kakhandako kakungolira. +Utsi wokhetsa msozi. Kodi amenewonso amagula chimanga mozemba pa ka Admarc kopanda kanthu kayandikana ndi khotilo? Sipadatenge nthawi, tidamva kuti mayi woyembekezera uja adathamangira nyumba ina ndipo chifukwa cha mantha adabereka mwana ngakhale nthawi yake idali isadakwane. +Nthawi yonseyo nkuti apolisiwo atakhamukira malo otsikira basi. Adali kukwapula aliyense. +Mwaotcha khoti, tiotchanso kamsika kanuka! Mwaiputa dala dungulinya, adatero mmodzi mwa alonda a bomawo, uku akukwapula mayi wina amene adatsika minibasi. +Tiyeni tsikani minibasiyo. Mukangotsika muzithawa. Mwagenda kupolisi muli ndi chamba mthumba! adatero wapolisi wina. +Abale kodi anthuwa ndimayesa timawalipira ndife kuti azititeteza? Onani lero akutikwapulanso popanda chifukwa. Bwanji osafufuza amene aotcha khotilo? adatero Abiti Patuma. +Mnzanga ndiye adandipezera Sylvester Namiwa, mneneri wa pulezidenti Peter Mutharika lero ndi wokondwa kwambiri kuti ukadaulo wa mtolankhani wa Nation, Albert Sharra, wamupatitsa mkazi amene adamanga naye ukwati pa 12 March 2016. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Namiwa akuti zonse zidayambika pamene iye adadwala, umotu ndi mu 2009 akukhala ku Malangalanga mumzinda wa Lilongwe. +Sylvester ndi Molly tsiku la ukwati wawo Panthawiyo, Namiwa mnzake wapamtima, Sharra, akuti adapita kukamuona ndi kumuguliranso mankhwala. +Poona momwe Namiwa amavutikira chifukwa ankakhala yekha, Sharra adamulangiza kuti apeze wokhala naye, ngakhale panthawiyo Sharra sadamasule thumba la tambe. +Koma Namiwa akuti adamufunsa Sharra mozizwa ndi malangizo ake: Ndani angandilole, ayise, taona momwe ndikuvutikira ndiye angandilole ndani? Macheza a awiriwa akuti adathera pa njole ina yotchedwa Molly Kenamu yomwe panthawiyo imakhala moyandikana nyumba ndi Namiwa koma kwawo ndi ku Bawi, kwa Senior Chief Makwangwala mboma la Ntcheu. +Ndidamuuza Sharra kuti namwaliyu sangalole kukhala pa ubwenzi ndi ine, adatero Namiwa. +Koma Sharra, malinga ndi ukatswiri wake ngakhale nayenso sadakwatire, akuti adauzitsa Namiwa kuti zitheka. Njira adazipezadi Sharra ndipo ndi madzi amodzi, Molly adamwetulira. Osadziwatu kuti Sharra panthawiyo adali atakambirana naye kale Molly, adatero Namiwa. +Namiwa akuti sadavutikenso kusula mbalume chifukwa Sharra adali atakonza kale kapansi ndipo pakutha pa sabata ziwiri Molly adali atazizira nkhongono kuvomereza kuti asamala Namiwa mpaka mmanda. +Chibwenzi chidayamba mu March 2010, mu July ndidamutenga kuti makolo anga akamuone. Chinkhoswe tidapanga pa 5 August 2010 ndipo nthawi yomweyo ndidamutegeratu. Pano tili ndi mwana wamkazi, Mwakamwereti, yemwe ali ndi zaka 5, adatero Namiwa. +Koma Sharra akuti Namiwa amafuna akhazikike kotero amafunika mkazi woti akwaniritse loto lake. +Ndinadziwa kuti Molly ndi mkazi yekhayo amene akadakwaniritsa khumbo lake ndipo ndine wokondwa kuti zili chonchi, adatero iye. +Akati tonde azimveka fungo akutanthauzanji? Miyambi ilipo yosiyanasiyana ndipo ina ukaimva mutu umachita kuwira, kulephera kulumikiza mwambiwo ndi tanthauzo lake. Ena amangoti bola ndanenapo mwambi osalingalira kuti kodi omvera akutengapo phunziro lanji pamwambiwo. Mwambi watitengera pabwaloli lero ndi wakuti tonde azimveka fungo. STEVEN PEMBAMOYO adakumana ndi mfumu Thipwi ya ku Nkhotakota kwa T/A Kanyenda pamsonkhano wokhudza za katetezedwe ka chilengedwe pomwe padatuluka mwambi wozunguawu ndipo adacheza motere: Ndikudziweni, wawa. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ine ndine Village Headman Thipwi wa mdera la gogochalo Kanyenda mboma lino la Nkhotakota. +Pamsonkhano walero mumabwerezabwereza mawu oti tonde azimveka fungo, mumatanthauzanji ndi mauwa? Choyamba mudziwe kuti mawu amene aja ndi mwambi chabe ndiye monga mudziwa mwambi umanenedwa ndi cholinga choti omvera atengepo phunziro kapena chenjezo malingana ndi zomwe zachitika kapena zikuchitika. +Nanga poti pamsonkhano umeneuja padali anthu okhaokha padalibe mbuzi? Nchifukwa chake mawuwo akutchedwa kuti mwambi, kutanthauza kuti sakuimira munthu aliyense, ayi, koma kuti pali phunziro lomwe tikufuna kuti anthu atolepo. Mwachitsanzo, msonkhano udali wokhudza za katetezedwe ka chilengedwe pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana ndiye mwambi umene uja udali woyenerera kuugwiritsa ntchito. +Nanga mwambiwu umatanthauzanji? Chabwino, mwambi umenewu umatanthauza kuti ntchito zamanja za munthu ndizo zimamuchitira umboni. Ngati munthu ali wolimbikira, zotsatira za kulimbikira kwakeko zimafotokoza zambiri za iye popanda wina kuima pachulu nkumalalika. Mwachitsanzo, mlimi wolimbikira amadziwika kuti ngolimbikira potengera zokolola zake, chimodzimodzi katswiri wa mpira wosewera kutsogolo amadziwika kaamba komwetsa zigoli. +Kutanthauza kuti mbuzi nchitsamba chabe chongobisalirako? Ndi momwemo ndithu, sikuti timatanthauza kuti munthu yemwe tikukambayo ndi tonde poti akumveka fungo la mbuzi, ayi. Iyi ndi njira chabe yoperekera phunziro kapena malangizo ndi chilimbikitso moti apo anthu omwe adali pamsonkhanowu adziwa kuti aliyense pamenepanja azilingidwa ndi zotsatira za ntchito zake, osati kungokamba pakamwa, ayi. +Ndiye tonde zikumukhudza bwanji pamenepa, osasankha nyama zina bwanji? Tondeyo ali ndi mbali yake yomwe amagwiritsidwira ntchito. Nkhani yaikulu ndi yakuti mkhola la mbuzi mukamabadwa ana pafupipafupi, ulemu umanka kwa tonde chifukwa ndiye amagwira ntchito mmenemo. Tonde akakhala wolephera kapena kuti ofooka, khola limakhala pomwepomwepo asasuntha, ayi. Ndiye mlimi akaona kuti zaka zikutha mbuzi zake sizikuswana, amakabwerekera tonde wina, uja nkumuchotsamo mwina kumugulitsa kwa mabutchala. Apa ndiye kuti amene uja sadamveke fungo chifukwa tonde mnzakeyo akangolowa mkhola nkuyamba kubereketsa, amalandira matamando kuti ndiye tonde chifukwa zipatso zake zikuoneka. +Ndiye kuti aja amati akamva fwemba la munthu nkumati tonde azimveka fungo amalakwitsa? Kwambiri, chifukwa potero paja sipayenera kugwiritsidwa ntchito mwambi umenewu. Atapeza mwambi wina bola monga mwambi wakuti wakumba kanyimbi chifukwa apo zikugwirizana poti kanyimbi naye ali ndi fungo vloboola mmphuno osati masewera, ndiye ngati munthu akumveka fungo losakhala bwino monga mwaneneramo kuti fwemba ndiye kuti akuononga mpweya ndipo anzake akuzunzika ngati momwe amazunzira kanyimbi. +Amuganizira kupha apongozi ndi mpeni Madzi achita katondo mmudzi mwa Chibwana kwa T/A Mankhambira, mboma la Nkhata Bay komwe mayi wina wa zaka 27 akumuganizira kuti wabaya ndi kupha apongozi ake a zaka 64 ati kaamba koti adatengapo gawo pothetsa banja lake. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mneneri wa apolisi mbomali, Ignatious Esau, watsimikiza kuti apolisi atsekera mchitokolosi Sylvia Chirwa ndi kumutsekulira mlandu womuganizira kupha Leah Banda mosemphana ndi ndime 209 ya malamulo a dziko lino. +Chirwa adaonekera bwalo la milandu la Nkhata Bay Lachitatu komwe mlandu wake adaupereka mmanja mwa bwalo la milandu lalikulu chifukwa mabwalo a majisitireti saweruza milandu yakupha. +Pakadalipano Chirwa ali palimandi kundende ya Nkhata Bay. +Esau wauza Msangulutso kuti Chirwa adagwidwa pomwe singanga yemwe adathamangirako pofuna mankhwala oti apulumuke ku mlanduwu adaulula. +Akumuganizira kuti adapha apongozi ake: Chirwa Malinga ndi kufufuza kwathu, Chirwa adalongosolera singangayu kuti wapha munthu ndipo amati akufuna mankhwala oti asakhale ndi mlandu. Singanga nkhaniyi idamukulira ndipo adauza anthu ena omwe adadziwitsa ife apolisi, adalongosola Esau. +Iye adati apolisi adamukwidzinga nawo unyolo woganiziridwayu ndipo pakadalipano ali palimandi kundende ya Nkhata Bay komwe akudikira kuti azengedwe mlandu wopha munthu, womwe chilango chake ndi kunyongedwa kapena kukhala kundende moyo wako wonse ukapezeka wolakwa. +Polongosola momwe nkhani yonse idayendera, Esau adati mwana wina wa mayi adaphedwayo, Lloyd Nkhata, adauza apolisi kuti Chirwa adakwatiwa ndi mchimwene wake yemwe amakhala mdziko la South Africa kwa zaka 9. +Iye adati awiriwa ali ndi mwana mmodzi wa zaka zisanu. +Esau adati kaamba ka mavuto ena awiriwa adasiyana ndipo Chirwa adabwerera kumudzi ndipo mmbuyo muno naye mwamuna wake wakaleyu adafunsa mayi ake kuti ampezere mkazi wina. +Mayiwa adapezadi mkazi wina, zomwe sizidasangalatse Chirwa. Akuti chibwerereni kuchokera ku Joni, Chirwa wakhala akuopseza kuti athana nawo apongozi akewo chifukwa adatengapo gawo pothetsa banja lake, adatero Esau. +Iye adati mauwa adapherezera usiku wa la Mulungu lapitali pomwe Chirwa adauyatsa ulendo wa kwa apongozi akewo ndi kuwabaya ali mtulo. +Adatsimikiza za kugwidwa kwa Chirwa: Esau Adawabaya pamimba, atatha apo adabayanso malo anayi cha kumsanaku ndipo Banda adamwalirira mnjira popita kuchipatala chachikulu cha Nkhata Bay, komwe nawo achipatala adatitsimikizira kuti adafa chifukwa chotaya magazi, adalongosola motero mneneri wa apolisiyu. +Lachinayi msabatayi Msangulutso udacheza ndi mfumu yaikulu Mankhambira yomwe idaperekeza malemuyo kuchipatala. +Ife tidali kunyanja usiku wa la Mulungu, pomwe tidamva kulira ndipo titathamangirako tidauzidwa kuti munthu wapha mayi Banda akugona kuchipinda, idalongosola motero mfumuyo. +Chibwana adati mwana wa mayiyo ndiye adawapeza mpeni uli kumsanaku. +Tidawatenga ndi kuthamangira nawo kuchipatala idalongosola mfumu Mankhambira, koma foni idadukira panjira ndipo kuyesayesa kuimbanso sadapezekenso. +Apalamula poitana T/A kumwambo pafoni Mwambo wobzala mitengo ku Bula mboma la Nkhata Bay udasokonekera Lachinayi pamene mfumu yaikulu Mbwana idakana kupita kumwambowu ati kaamba koti okonza mwambowo sadatsate dongosolo loitanira mfumu. +Mwambowu, womwe adakonza ndi a nthambi ya zankhalango mogwirizana ndi bungwe la Temwa, udaima ndi pafupifupi mphindi 30. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Apatu nkuti akuluakuluwo akukambirana za tsogolo la mwambowo ndi wapampando wa chitukuko kumeneko, Ivol Nyirenda, yemwe adabweretsa uthengawo. +Mlendo wolemekezeka pamwambowo, yemwe ndi wapampando wa khonsolo ya Nkhata Bay, Hastings Mkandawire, pamodzi ndi akuluakulu ena a boma, adangoti kakasi kusowa chochita poti zawo zinali zitada. +Nawo ana asukulu pamodzi ndi anthu ena onse oitanidwa adali nyominyomi pamalopo, pomwe ena adangokhala pansi kudikira za zotsatira za zokambiranazo. +Uwutu udali mwambo waukulu wokhazikitsa nyengo yobzala mitengo mchigawo cha kumpoto. +Koma nkhope za anthuwo zidawala patatha mphindi 30 pomwe adaona T/A Mbwana ikutulukira mgalimoto ya mtundu woyera. Mukucheza kwathu ndi Mbwana, mfumuyi idakana kukambapo zambiri pankhaniyo ati pokana kuwaika mmavuto omwe adakonza mwambowo. +Afunseni omwe akonza mwambo uno, ndikayankha ine, ndingawaike mmavuto, idatero mfumuyo. +Koma Mkandawire, yemwe adabweretsa uthengawo, adati anthuwo sadatsate dongosolo poitana mfumuyo kumwambowo. +Simungaitane mfumu kumwambo ngati uno kudzera palamya, iye adatero. +Ndipo polankhulapo, mmodzi mwa okonza mwambowo, woimira DC wa boma la Nkhata Bay, Mzondi Moyo, adati zoti dongosolo silidatsatidwe sizidali zoona. +A kunthambi ya zankhalango adatsata dongosolo poitana mfumuyi komanso tidapereka udindo woitana mfumuyi kwa a bungwe la Temwa omwe amakhala nayo pafupi kwambiri, adatero Moyo. +Mitengo yokwana pafupifupi 8 miliyoni ibzalidwa chaka chino mnyengo yobzala mitengo mchigawochi. +Othawa nkhondo ku Mozambique asamukira ku Neno Bungwe lothandiza anthu othawa kwawo pazifukwa zosiyanasiyana la UNCHR layamba kusamutsa anthu othawa nkhondo ku Mozambique kupita ku Luwani mboma la Neno. +Anthuwa, omwe akuthawa nkhondo yapachiweneweni, amafikira kumisasa yongoyembekezera mmaboma a ku Nsanje, Chikwawa, Mwanza komanso Neno omwe achita malire ndi dziko la Mozambique. +Escom in free-for-all fuel scam Wait gets longer Secrecy over party funders Bungwe la UNHCR lidayamba kusamutsa othawa nkhondowa sabata ziwiri zapitazi pamene anthu 81 adawapititsa ku Luwani mboma la Neno kuchokera kumalo omwe amangodikirirapo ku Nsanje. +Ena mwa othawa nkhondo ku Mozambique ulendo wa ku Luwani Mkulu wofalitsa nkhani kubungweli mMalawi muno, Kelvin Shimoh, adati cholinga chawo ndi kuti othawa nkhondowa akhale malo amodzi komwe angakalandire thandizo lokwanira. +Iye adati pali pafupifupi anthu okwana 11 000 omwe athawa nkhondo kuchokera ku Mozambique ndipo chiwerengerochi chikuyemebezeka kukwera kwambiri. +Ku Kapise mboma la Chikwawa kuli anthu pafupifupi 10 000 ndipo akuyembekezeranso kusamutsidwa kupita ku Luwani komwe kuli malo abwino okhala, olandirira thandizo la mankhwala komanso sukulu zoti ana omwe ndi ambiri azikaphunzirako. +Mkulu wina wa bungwe lomweli la UNHCR woona za chitetezo cha othawa kwawo, Elsie Bertha Mills-Tettey, wapemphanso dziko la Malawi ndi anthu onse kuti asawasale anthuwa powaganizira kuti ndi achiwembu. +Kafukufuku wathu wapeza kuti anthu othawa nkhondowa ali pachipsinjo choopsa chifukwa ataya katundu wawo, abale awo ena aphedwa akuona, komanso ena mwa iwo apulumuka atazunzidwa, adatero Mills-Tettey. +Iye wayamikiranso bungwe la Unicef pachithandizo chomwe likupereka kwa anthuwa nkhondowa, makamaka ana, pankhani zowambikitsa kuti apitirizebe maphunziro awo. +Za kulephereka kwa zisankho Muzina Edi mwana Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Edi sebe santu Muzina zizata mfana Ya muzina Sindikudziwa ngati Papa Wemba nyimboyo adaimverapo koma ndimo ndinkayimvera pamene inkaphulika malo aja timakonda pa Wenela. Gervazzio ndiye adaika nyimboyo pokumbukira Papa Wemba amene watsikira kwachete. +Koma dziko ili! Zoona likutenga anthu ofunika ndi otchuka, achina Prince, kusiya ife ojiya, osolola ndi osenza pano pa Wenela. Imfa ikusiya zilengwalengwa. +Tsiku lina ndidzaipha imfa yotenga mayi kusiya mwana akulira. +Tsikulo wina adati ndipite ndikaitanire ku Mibawa. Koma nkadadziwa kuti amandikankhira kunkhondo! Padafika asirikali atavala nkhwani-nkhwani. Komatu eni minibasi samaimva, ati khobwe akatolera kuti? Nawo adabwera ndi mapanza awo, inde magigo. +Sitiimva. Minibasizi ndi zanu kuti muzitolera ndalama? adatero phanza wina, atanyamula miyala. +Kupanda nzeru. Malowa ndi anu? Kodi ogulitsa nkhwani mumsika angamemane kuti azitolera ziphaso ndiwo chifukwa nkhwaniwo ndi wawo? Kupusa! Mnyumba ya mwini saotchera mbewa, adatero wapolisi wina, akukanyanga mmodzi mwa magigowo nkumuponya mchimbaula adachilawa Chihana. +Apo ndeu idabuka koma paja lamulo liposa mphamvu, akhonsolo adawina ndipo adayamba kutolera ndalama kuchokera kwa madalaivala. +Nditabwerera ku Wenela, ndidapeza Abiti Patuma ndi ena onse akumvetsera wailesi. +Chisankho chimati chikhalepo ku Mchinji chalephereka. Boma silidapereke ndalama ati chifukwa lilibe, adatero muulutsi. +Boma lilibe ndalama bwanji? Koma chisankho cha ku Zomba ndiye adapeza ndalama? Pafa khoswe apa, adatero Abiti Patuma. +Paja nawe, kumangomva fungo la khoswe paliponse? Kulitu njala uku, adatero bambo amene adali naye tsikulo. +Zanu. Komabe inetu ndikuona kuti Dizilo Petulo Palibe ikuona kuti kuchititsa chisankho ku Mchinji kukhoza kuchititsa Male Chauvinist Pigs kuoneka mashasha, adayankha Abiti Patuma. +Abale anzanga, musandifunse amatanthauzanji chifukwa nane sindikudziwa. Pajatu ine za matchera ayi. +Padakalipano boma likuphwanya malamulo omwe amaneneratu kuti chisankho chiyenera kuchitika pasanathe masiku mwakuti, adatero Abiti Patuma. +Mukutayatu nthawi. Paja zomatiuza kuti chakuti chichitike pofika tsiku lakuti si mbali yathu, adatero bambo adali naye uja. +Mukutanthauza kuti nthawi yokhala pampando ikadzatha, Mustafa sadzafuna kubweza mpando kwa Ajibu? Adangoti duuu mkulu uja. Adalandira foni. +Mwati bwanji? Shati Choyamba watisiya? Zabodza izo, nkadamva. Ndikudziwa kuti ali ku Tajkstan komwe amuchotsa dzino dzana. Kukonda kupekera ena imfa bwanji? Akukupanitu makofi akabwera, adatero mkuluyo adatero. +Imeneyinso idandipita. Malingaliro adali kwa Papa Wemba komanso Prince. +Zikhulupiriro zina Zisokoneza mdulidwe Zikhulupiriro zosiyanasiyana zikusokoneza ntchito ya mdulidwe wa abambo womwe unduna wa zaumoyo komanso mabungwe akulimbikitsa, Msangulutso wapeza. +Escom in free-for-all fuel scam Wait gets longer Secrecy over party funders Ku Nsanje, Dowa komanso ku Nkhata Bay ndi maboma ena amene zikhulupirirozi zachititsa kuti abambo asamapite kuchipatala kukalandira mdulidwewu. +Malinga ndi Senior Chief Dzoole ya mboma la Dowa, anthu ati samvetsa komwe kumapita kachikopa kamene adulako, zomwe zimawapatsa mantha. +Anthu amaganiza kuti kachikopa kamene akadulako amakakachitira mankhwala. Maganizo awa ndi amene amachititsa anthu kuno kuti asapite kukalandira mdulidwe. +Komanso anthu okwatira amaganiza kuti pamene akalandira mdulidwe, ndiye kuti akazi awo aziwayenda njomba chifukwa akawadula sangakakhale malo amodzi ndi mkazi wawo, ati panthawi iyi amaganiza kuti mkazi wawo akhoza kuawayenda njomba, adatero Dzoole. +Mdulidwe wa abambo wakuchipatala ndi njira imodzi yothandiza kupewa kufala kwa HIV Dzoole adati mdera lake, mwa amuna 10, amuna anayi okha ndi amene amalandira mdulidwe. +Kampeni ili mkati moti mafumufe atiphunzitsa kuti timeme anthu akachititse mdulidwe, koma ndi amuna ochepa amene akupita kukalandira mdulidwe, adatero Dzoole. +Senior Chief Kabunduli wa mboma la Nkhata Bay wati kampeniyi yakanika kumeneko chifukwa anthu amaganiza kuti akakalandira mdulidwe ndiye kuti alowa chipembedzo cha Chisilamu. +Ambiri kunoko amaganiza kuti amene alandira mdulidwe ndiye kuti ndi achipembedzo cha Chisilamu. Maganizo amenewa ndi amene akuchititsa kuti anthu asakhale nazo chidwi zokalandira mdulidwezo, adatero Kabunduli. +Titafunsa mfumuyi ngati ikumemeza anthu ake kuti akachititse mdulidwe, iyo idati: Ukawauza kuti kachitsitseni mdulidwe, akufunsa ngati iweyo unapanga. Ndiye ine pa msinkhu wangawu sindingapite kumdulidwe. +Ndinetu munthu wamkulu, ndiye ndikakalandira mdulidwe lero, balalo lidzapola liti? ..sindingapange zimenezo komanso kampeni imeneyi ine sindikuchita nawo. +Ku Nsanje, malinga ndi McKnowledge Tembo, HIV/Aids co-ordinator pachipatala cha boma, zikhulupiriro za anthu kumeneko zimati munthu akalandira mdulidwe ndiye kuti amaafooka kuchipinda. +Kunoko tinaphunzitsa mafumu, amipingo ndi azaumoyo za ubwino wa mdulidwe, koma mukamayenda muja, anthu amafunsa zambiri zokhudza zikhulupiriro zawo ndi mdulidwe. +Palibe amene adabwera poyera kudzatiuza kuti akufooka kuchipinda chifukwa walandira mdulidwe. Komabe anthu upeza akulankhula, ndi zabodza ndipo palibe umboni wake. Zoona zake nzoti macheza amakhalanso bwino mbanja mwamuna akakhala kuti adalandira mdulidwe, adatero Tembo. +Nayenso Simeon Lijenje wa PSI akuti ndi bodza la mkunkhuniza kuti amuna amene alandira mdulidwe amafooka ndipo wati amuna amene adulidwa ndiwo amachitanso bwino kuchipinda kusiyana ndi osadulidwa. +Palibe umboni wa zomwe anthuwo akunena. Dziwani kuti mwamuna amene walandira mdulidwe ndiye amasangalala kuchipinda chifukwa amakwaniritsa bwino chilakolako cha mkazi wake, adaphera mphongo Lijenje. +Iye adati kampeni ya mdulidwewu idayamba mu 2012 ndipo kuchokera mu October 2014 mpaka September 2015 pafupifupi abambo 93 642 ndiwo alandira mdulidwe mbomalo. +Achipatala amati ngati abambo alandira mdulidwe, ndiye kuti pali mwayi woti chiwerengero cha anthu otenga kachilombo ka HIV podzera mkugonana chingachepe ndi anthu 6 mwa 10 alionse (60%), malinga ndi mabungwe a WHO komanso UNAIDS. +Kuyambira mu 2007, mabungwewa akhala akubwekera kuti mdulidwe umathandize kwambiri kuti kachilomboka kasafale kwambiri. +Malinga ndi mabungwewa, maiko 14 a kummwera kwa Afrika komanso kummawa, ndiwo ali kalikiriki kupangitsa kampeni kuti amuna azikalandira mdulidwe. +Mdulidwe wa abambo ndi pamene achipatala amadula kachikopa kakutsogolo kwa chida cha abambo. Kachikopaka kamasunga zoipa, koma ngati walandira mdulidwe, amakhala waukhondo. Zoipazo zimakhala zasowa malo oti zisungidwenso, lidatero lipoti la UNAids, nkuonjera kuti mdulidwe umathandiza kuchepetsa matenda a khansa ya khomo la chiberekero cha amayi. +Ngakhale ngamba ikuwaula mmera, akuchilimikabe Nkhani ya ngamba siyochita kufunsa chifukwa momwe zikuwaukira mbewu mminda ndiumboni wakuti dzuwa lalanda malo a mvula. Alimi ambiri pano manja ali mkhosi ndipo ena angofika potailatu mtima. Ngakhale zinthu zili choncho, alimi ena sakugonja ndipo akuti sangachoke mmunda pokhapokha ataona kuti mbewu yomalizira yauma ndi dzuwa. Loveness Billy a ku Salima ndi mmodzi mwa alimi olimbika chonchi ndipo STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere: Escom in free-for-all fuel scam Wait gets longer Secrecy over party funders Mlimiyo pakati pa munda wake wochititsa chidwi Moni mayi komanso ndikudziweni. +Ndili bwino. Dzina langa ndi Loveness Billy ndimachokera mmudzi mwa Mjunga ku Salima. +Tsono pamenepa mukutani? Apa ndikupala udzu mchimanga mwangamu kuti chikule bwino mosanyozoloka chifukwa chosokonezedwa ndi udzu kapena zomera zomwe si gawo la mbewu zanga. +Komatu chimangachi chikuoneka ngati palibepo chomwe mungatole ndi mmene chaumiramu. +Anthu owonanu mukuganiza choncho koma mwini wakene ndikuona kuti chiyembekezo chikadalipo. Mvula itangoti ibwere mukhoza kuona mmene chinganyamukire. Mmene ndikupala chonchimu, zindithandiza kuti chinyontho chochepa chomwe chilipo mnthakamu chigwire ntchito ku mbewu zokha osati kulimbirana ndi udzu. +Mesa boma likuti ndi mmene zinthu zililimu mukuyenera kukangalika ndi mbewu zina zopirira ku ngamba? Zimenezo tikutsatiranso moti chakumunsi kwa mindayi kuli madimba komwe tagaula kale ndipo pompano tikabzalako mbewu zinazo monga nyemba, kachewere, mbatata ndi chinangwa. Chinangwacho ndiye tidabzala kale koma pano tikufuna kukabzala mbatata chifukwa timasakasaka mbewu ndiye yapezeka. +Alimi anzanutu atambalala kusungira mphamvu kuti mvula ikagwanso adzaunde mizere ya mbatata kapena chinangwa. +Ayi amenewo ndiwosamvetsa chabe chifukwa ngakhale a bomawo sakunena kuti tizule kapena kunyanyala chimanga koma kuti pambali pa chimangacho tibzalenso mbewu zina. Palibetu vuto kusakaniza mbewu zinazo ndi chimanga makamaka pomwe malo ali ochepa. Mwachitsanzo, munthu akhoza kubzala mbatata mmphepete mwa mzere wa chimanga. Chimanga chikakula pangono amatenga mbewu ya mbatata nkubzala ndipo zonse zimakula bwinobwino. +Inu mumachitaponji pa zaulimi wa mthirira? Ulimi umenewonso timapanga mchilimwe. Tidakumba madamu okololeramo madzi omwe timagwiritsa ntchito kuonjezera omwe timapatutsa mumtsinje chifukwa mtsinjewo pena madzi amachita kutheratu nanga ogwiritsa ntchito si ambiri kuyambira kumtunda komwe udachokera mpaka kumunsi. +Mwakonzekera bwanji ulimi wa mthirira? Pakadalipano tikuyanganabe zipangizo zina makamaka mbewu ndi feteleza koma zina monga madzi ndi muja ndafotokozera kale kuti kupatula mumtsinje, tili ndi madamu okololera madzi. Ikakhala ntchito ina monga kugaula ndi kuunda mizire ziri mkati mmadimba ena pasi pakadali pofewa. +Kugawuliratu pano ndiye podzafika chilimwe sipadzakhala patalimbaso? Ayi timalawirira kukatchefula mvula ija ikangotha pansi pakayamba kuchita mbuuu. Siyikhalanso ntchito yowawa komanso tikatero timadzipatsa mpata wokwanira wothira manyowa kuti ndi chinyontho chija, dothi ndi manyowawo zilowererane bwino. +Inu mungawauze chani alimi anzanu omwe ataya mtima? Asataye mtima koma akhale ndi chikhulupiliro zonse zidzakhala bwino. Vuto ndilakuti akatambalala, pomwe mvulayi idzabwerenso adzakhala ndi chintchito chachikulu. Chofunika nkungosamala mbewu zomwe zidamera kalezi nanga sipadalowa kale zambiri. Mvula ikadzabweraso tizidzangopakiza momwe mbewu zaferatu. +Kodi Idrissa Walesi akutani mu Mozambique? Mu 2012 ku Mighty Wanderers kudatchuka wosewera wa kumbuyo, Idrissa baba Walesi. Atangotchuka, Walesi adasowa ndipo zidamveka kuti wakwawira ku Mozambique. Chipitireni mu 2014, Walesi adachita zii! Kodi akusewera? Kapena wayamba geni? BOBBY KABANGO adamupeza mumzinda wa Nacala Provincia mdziko la Mozambique ndipo acheza motere; Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Idrissa Baba Walesi ulipo? Ah achimwene, ndilipo ine. Mwasowatu Ukutani mdziko la Mozambique? Walesi akudya bwino ku Mozambique Pajatu chibwerereni kuno mu 2014 ntchito yanga ndi yampira basi. Kuchokera pa nthawiyo ndakhala ndikusewera timu ya Desportivo mpaka lero pamene ndasintha timu. +Koma umasewera nthawi yonseyi? Kapena ku training kokha? Haha mwandinyozatu achimwene. Ndakhala ndikusewera pafupifupi gemu iliyonse. Chaka changothachi adandisankha ku timu kwathu kuti ndatchinga bwino kumbuyo. +Chibwerereni ku Mozambique, timu yako yasewera bwanji? Chaka chathachi ndiye sizidayende, tathera pa nambala 12 ndi mapointi 29. +Chachitika nchiyani kuti uchoke ku timuyi? Tidali pa mgwirizano wa zaka ziwiri, mgwirizano watha koma adandipempha kuti ndisewererebe timuyi koma ndakana chifukwa timu yomwe ndapita panoyi idandilonjeza zochuluka. +Timu yanji? Ndipo uzilandira zingati? Ferroviario De Nacala yomwe idathera pa nambala 8. Achimwene mpaka ndinene malipiro? Aah ayi koma inu nokha mutha kudziwa koma musalembe. Koma ndayamba timu imeneyi chaka chatha ndipo tili pa mgwirizano wa chaka chimodzi kuchokera pa 26 February 2016. +Ndinkafuna mkazi wamakhalidwe Ronald Mwandama amene amakhala mdera la Bangwe ku Blantyre adakhala zaka ziwiri wopanda wapambali atamwalira mkazi wake. Mu 2014 adapalana ubwenzi ndi Annie Kalambo yemwe amachokera mmudzi mwa Sayiko, T/A Santhe mboma la Kasungu, yemwe nayenso bambo wakunyumba adatsikira kuli chete. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ronald akuti adali akuwunguza mkazi woti amange naye banja kutsatira imfa ya mkazi wake ndipo samangofuna munthu wamba koma mkazi wamakhalidwe abwino. +Ronald ndi Annie pano ndi thupi limodzi Pafupi ndipo uli. ndinasaka mu Bangwe momwemuno mkazi wamakhalidwe omwe ine ndimafuna. Pomuona Annie, mtima unakhutira ndipo ndinayamba kusaka nambala ya foni yake. Ndinatumiza uthenga wa pafoni (SMS) yokamba zaubwenzi womwe udzathere mbanja, adatero Ronald. +Iye adati sizidali zophweka kuti Annie avomere pempho lake chifukwa zidatenga miyezi kuti ayankhe uthengawo. +Poti ndinafunitsitsa, ndinangoyimbano foni ndipo adati tikumane. Ine mtima udagunda kwambiri, si wokakanidwa uwu! Koma poti ndinali nditachipempherera kuti ndipeze mkaziyu, bambo, Ambuye adanditsogolera ndipo ubwenzi nkuyamba, adafotokoza Ronald. +Annie naye anati zinali zomuvuta akaganizira za t sogolo la ana ake omwe bambo awo adatisiya. +Ine ndi mayi ndiye uthengawo umafuna nthawi yokwanira kuwuunika. Sindinafune kuzunzitsa ana kaamba ka mwamuna. Koma Ronald analimbikira ndiye ndinati mwina ndi Mulungu, chofunika ndiyankhe pempho lawo, adatero Annie. +Iye akuti sadabise mawu kukhosi oti ali ndi ana, naye Ronald adati ali ndi ake. +Tili mkati mocheza kuchokera 2014 kufika mu December 2015 ndinaona kuti Ronald ndi bambo wokonda ana, achibale ndiponso woopa Mulungu. Kwawo kuli ana ndi zidzukulu ndi anga tiwalere limodzi motsogozedwa ndi Mulungu, adafotokoza Annie. +Ronald ndi Annie pano akwanitsa miyezi isanu ndi umodzi ali mbanja. +Anatchezera Sakuthandiza mwana Agogo, Ndine mtsikana wa zaka 19 ndipo ndili ndi mwana mmodzi. Ndidali pabanja koma litatha bambowo samatumiza chithandizo olo sopo. Ndiye nditani poti mwanayu ndimavutika naye ndekha? Pepa mtsikana, Ndi zimene ndakhala ndikulangiza atsikana nthawi zonse kuti limbikirani sukulu mudakali anthete, osati kuthamangira kukwatiwa! Tikamanena kuti si bwino kuthamangira banja timadziwa kuti nthawi zambiri zotsatira zake zimakhala ngati zimene wakumana nazo iwezi. Tsono nkovuta kukuthandiza zenizeni chifukwa sukulongosola kuti ukwati wanu udali wotani-wongolowana, wachinkhoswe kapena mudadalitsa kutchalitchi? Nanga zifukwa zomwe banja lako lidathera nzotani? Ukwatiwo udathera kuti-kukhoti kapena basi mwamuna adangoti zipita kwanu? Ngati ukwati wanu udali ndi ankhoswe, iwo akutipo chiyani pa kutha kwa ukwati wanu? Banja lenileni silimangotha lero ndi lero popanda zifukwa zenizeni; banja si masanje. Ndiye mmene zikuonekera inu mudangotenganapo popanda ndondomeko yeniyeni ndipo mwamuna adalola zokukwatira pothawa milandu atakupatsa pathupi, si choncho? Ndiye poti amati madzi akatayika saoleka, chomwe ungachite nchoti nkhaniyi upite nayo kwa ankhoswe kapena kubwalo la milandu kuti akakuthandize chifukwa bamboo wa mwana ali ndi udindo woti azithandiza mwana wake ngakhale kuti banja lanu latha. Mwana asavutike chifukwa cha kusemphana Chichewa kwa inu makolo. Kodi, sukulu udalekeza mukalasi yanji? Chonde, ngati pali mwayi woti nkubwerera kusukulu, chita zomwezo chifukwa udakali mwana wamngono. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndikhulupirire? Anatchereza, Ndidali ndi chibwenzi chomwe tinkakondana kwambiri ndipo tinkamvanadi koma titakhala zaka ziwiri osaonana kaamba ka zovuta zina popeza aliyense ankakhala ndi makolo ake. Koma panopa adakwatiwa ndipo ali ndi mwana mmodzi. Titakumana miyezi yammbuyomu adandiuza kuti amandikondabe. Kodi ndikhulupirire? Kapena ndipange bwanji? Ndithandizeni Anathereza. +Godfrey Richard Sindima, Thyolo Okondeka a Sindima, Tisatayepo nthawi apa. Si mwati adakwatiwa ameneyo ndipo ali ndi mwana mmodzi? Ameneyo si wanunso ayi, ndi mwini wake! Akadakhala kuti amakukondani akadakudikirani, osati kukwatiwa ndi munthu wina, ayi. Kodi mukundiuza kuti kuti kumene adakwatiwako adachita kumukakamiza? Padali chikondi pakati pa mwamunayo ndi mkazi yemwe mukuti adali chibwenzi chanuyo. Tsono inu musapusitsidwe kuti akukukondanibe pamene ali pabanja ndi mwamuna wina. Apa ndiye kuti dzanja silidalembe kuti iye adzakhala nthiti yanu. Funani wina, achimwene, ameneyo ngodanitsa. Mkazi wapabanja amene amadyeranso maso amuna ena timati ndi wachimasomaso ameneyo ndipo si wofunika kutaya naye nthawi. Ndikhulupirira mwamvetsa. +Amamumenya Zikomo Anatchereza, Ineyo ndili ndi chibwenzi ndipo timakondana kwambiri koma makolo ake amamumenya chifukwa cha ine. Ndiyeno ndikamuuza kuti chithe amakana, koma ineyo ndimaopa kuti adzamuvulaza. Nditani pamenepa? Ndimusiye? Pati bii pali munga! Makolo anzeru sangamamenye mwana wawo wamkazi popanda chifukwa. Zimene ukunena kuti amamumenya chifukwa ali mchikondi ndi iwe si zoona ayi, koma chilipo chifukwa chomwe amamumenyera. Mwina mwana wawoyo adakali pasukulu ndipo sakufuna kuti asokoneze maphunziro chifukwa chochita zibwenzi ali pasukulu; mwina nkutheka sakuvomereza chibwenzi chanu kaamba ka zifukwa zina ndi zina. Vuto ndi loti sukufotokoza bwinobwino za cholinga cha chibwenzi chanucho, msinkhu wako ndi zina zotero. Ngati chibwenzi chanucho cholinga chake nchoti mudzakhale pabanja, iwe wachitapo chiyani kuonetsa kuti si zachibwana ayi? Iwe udamaliza sukulu ndipo uli pantchito kapena ayi? Pali chitomero kapena ayi? Mwina utandiyankha mafunso amenewa ndingathe kuona kuti ndikuthandize bwanji. +Achita phwando ndi kuimitsidwa kwa Kuluunda Lero kuli madyerero mmudzi mwa Senior Chief Bibi Kuluunda mboma la Salima kusangalalira kuti mfumuyi yaimitsidwa kugwira ntchito yake mbomali. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Anthu a mmudzimu kuphatikizaponso mafumu ena akhala akubindikira kuofesi ya DC wa bomali pofuna kukakamiza boma kuti ichotse mfumuyi poiganizira kuti ndi yaziphuphu. +Anthuwa adayamba mbindikirowo pa 11 April wapiyatu. +Lachitatu lapitali mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adasayina kalata yoimitsa Kuluunda amene wakhala paufumuwu kwa zaka 20, kupereka chimwemwe kwa anthuwa. +Mtsogoleri wa anthuwa, Muhammad Chingomanje, adati chimwemwe ndi chosayamba. +Wayamba waimitsidwa ufumu: Kuluunda Lero [Lachinayi pa 5 May] lidzakhala tsiku lachimwemwe pamoyo wanga. Lero lidzakhala tsiku lapaderadera mmbiri ya dziko la Malawi, maka kwa ife anthu a ku Salima. +Titagona panja pa ofesi ya DC kwa masiku 24, lero yankho labwera. Aliyense ndi wokondwa komanso wachimwemwe ndi zomwe zachitika lero, adatero Chingomanje. +Kulankhula ndi Chingomanje pafoni kudali kovutirapo chifukwa cha nyimbo zomwe anthu amaimba komanso phokoso lachimwemwe lomwe limamveka. +Nyakwawa Chilaboto ya mwa Gulupu Kawanga mdera la Kuluunda, idati iye komanso mafumu onse 31 amene amachita nawo mbindikirowo ndi okondwa ndi ganizo la Mutharika. +Mtendere wadza mmudzi mwanga limodzi ndi anthu anga 1 800 amene ndimawalamulira. Takhala tikulira ndi mfumuyi kwa zaka koma maso athu adali kuboma kuti atiyankhe. Lero ndi chimwemwe paliponse, idatero mfumuyi uko akuimba nyimbo yachimwemwe. +Mfumuyi idati lero kukhala phwando chifukwa yankho labwera. Tikupha ngombe komanso mbuzi, tikhala ndi tsiku lalikulu Lamulunguli chifukwa zomwe timapempha zayankhidwa. +Aliyense abweretsa zakudya kusangalala kuti tsiku lomwe timaliyembekeza lakwana, adatero Chilaboto. +Iye adati monga mfumu, nkhani ya kuimitsidwa kwa Kuluunda ithandiza ntchito yake chifukwa kwa nthawi ndakhala ndikulimbana ndi amfumuwa pankhani zoti nanunso simungazimvetsetse. Nthawi yoti tipume yakwana tsopano. +Titaimbira foni Kuluunda kuti timve maganizo ake, adangoti: Ndili mminibasi ndiye sitingamvane. Mundiimbirenso. +Titaimbanso mfumuyi sidayankhe foni. +Malinga ndi nduna ya maboma aangono Kondwani Nankhumwa, Mutharika waganiza zoimitsa Kuluunda malinga ndi nkhani za katangale zomwe mfumuyi ikukhudzidwa nazo monga zoti idalandira K30 miliyoni ya Green Belt Initiative zoti igawire anthu okhudzidwa ndi polojekitiyi, koma sidalongosole komwe idapita K15 miliyoni. +Blessings Cheleuka wa pa JOY FM Amalawi ambiri kuyamba Lolemba mpaka Lachisanu nthawi ya 2 koloko kufika 4 koloko masana amatsegula wailesi ya Joy FM kuti amvere nyimbo zothyakuka zoimbidwa ndi Amalawi anzawo. Namandwa wophulitsa nyimbo zimenezi ndi Blessings Cheleuka, yemweso wachitapo mbali yaikulu kutukula alakatuli mdziko muno. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere: Cheleuka: Chilichonse nchotheka pamoyo wa munthu Dzifotokoze mkulu wanga. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ine ndine Blessings Cheleuka, ndimachokera mmudzi mwa Mothiwa kwa T/A Likoswe mboma la Chiradzulu. Ndine muulutsi wa pawayilesi komanso ndimakonda ndakatulo kwambiri. +Ntchito yakoyi udayamba liti? Ndakhala ndikugwira ntchitoyi kwa zaka 12 ndipo ndagwira mnthambi zosiyanasiyana monga wolemba nkhani, mkonzi, muulutsi ndi zina. China choti mungadziwe nchakuti ndagwirako ntchitoyi kunyuzipepala ndi kuwayilesi komwe ndiye ndili ndi ukadaulo kwambiri. +Akadaulo ambiri amakhala ndi komwe adaphunzirira ntchito, iwe udaphunzirira kuti? Choyamba, ndidaphunzira zautolankhani kusukulu yaukachenjede ya Polytechnic, nthambi imodzi ya University of Malawi. Kumeneku ndidaphunzira zomwe zimatenga kuti munthu ukhale mtolankhani mbali zonse. Kuchoka apo mmalo momwe ndakhala ndi kugwira ntchito monga Power 101 FM komwe ndidayambira ntchito; ndidaphunzirako za kuulutsa mapologalamu osanjenjemera chifukwatu kunena zoona ndi luso lapadera limenelija. Ndimayamikaso Mulungu ponditsogolera ndi kundiunikira. +Nanga umaulutsa mapologalamu anji pawailesi? Ndimaulutsa mapologalamu ambiri monga Dimba Music yomwe imauluka kuyambira Lolemba mpaka Lachisanu nthawi ya 2 koloko masana mpaka 4 koloko madzulo; Zina Ukamva yomwe imauluka 8 koloko madzulo Loweluka; pologalamu ya ndakatulo yotchedwa Patsinde yomwe imayamba 8 koloko mmawa mpaka 10 koloko; Mfuwu Wa Chimwemwe kuyamba 6 koloko mpaka 9 koloko mmawa Lamulungu; ndi Gospel Top 20 ya nyimbo za uzimu komanso ndine ndimayanganira za uwulutsi kuwailesi ndi kanema za Joy. +Ukutinso uli ndi chidwi pa zaulakatuli, umatengapo gawo lanji? Ndapanga zambiri monga kudzera mu pologalamu yanga ya Patsinde. Ndimafukula alakatuli omwe sadayambe kudziwika. Ndimakonzaso zochitika za alakatuli ndipo anthu ambiri amazikonda. +Ukafatsa umakonda kutani? Ndimakonda kuonerera mapologalamu a pakanema ndi zauzimu basi. +Mwina okutsata amangoti ndiwe muulutsi, ungawauzenji za iwe? Ine ndine Blessings Cheleuka odziwika kuti Bule wanu pazausangalatsi ndipo cholinga changa nkusangalatsa Amalawi basi. +Adali kasitomala wa mchemwali wanga Mchemwali asamangokhala wokuphikira nsima kapena kukuthandiza kuchapa zikavuta, nthawi zina azikhalaso njira yokulondolera njira ya komwe kuli mbali ya nthiti yako. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Umu ndimo zidakhalira pakati pa Daniel Gunya, wa mmudzi mwa Bubua, T/A Makwangwala mboma la Ntcheu, ndi Beatrice Kamwendo, wochokera kwa Mchela, T/A Mlumbe, mboma la Zomba. +Daniel akuti Beatrice amabwerabwera kumalo odyera a mlongo wake kudzagula zakudya ndipo awiriwo adayamba chinzake koma nthawi yonseyi akuti Daniel amangomezera malovu, osamasuka. +Daniel ndi Beatrice patsiku lomwe adachititsa chinkhoswe. Ukwati wawo udzamangidwa pa 29 October Iye akuti izi zidakhala zikuchitika kwa nthawi yaitali mpaka tsiku lina adatenga nambala ya lamya ya foni ya namwaliyo kwa mlongo wakeyo nkumuimbira ndipo umu ndimo adayambira kucheza. +Tidacheza ndithu kwa miyezi ingapo ngati munthu ndi mnzake mpaka mchaka cha 2011 pomwe ndidamutengera kumalo osungirako mbiri (Museum) komwe ndidamuuza zakukhosi kwanga ndipo ndidalumphalumpha mumtima atandivomera, adatero Daniel. +Iye akuti akaona Beatrice, amaona mnzake weniweni wokhala naye mpaka muyaya. Akuti amadzadza ndi chimwemwe komanso amapeza chilimbikitso cha mtundu uliwonse. +Beatrice akuti iye adali ndi malingaliro kuti Daniel adali naye nkhani chifukwa nthawi zonse akakumana kokagula chakudyako, Daniel amaonetsa nsangala yachilendo yosonyeza kuti waona chachikulu. +Iye akuti adaona mwamuna wachilungamo, wachikondi ndinso wodzichepetsa ndi wolimbika pochita zinthu ndipo izi zidamutenga mtima mpaka sadakaike konse kuti Mulungu ndiye adamutuma kuti azipita kumaloko. +Awiriwa adapanga chinkhoswe chawo pa 3 March chaka chino ku Nancholi ndipo pano adakonza kale tsiku la ukwati lomwe ndi pa 29 October cjaka chino pabwalo la zamasewero la College of Medicine mumzinda wa Blantyre. +Anatchezera Sagona mnyumba Anatchereza, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndili ndi zaka 20 ndipo amuna anga sagona mnyumba ndiye chonde, ndithandizeni. Akuti ndikawauza ankhonswe banja langa litha. Ukwati tapanga chaka chatha. Ndine A Blantyre Zikomo A, Mwamuna wakoyo ngwachibwana zedi! Mwangokwatirana kumene ndipo ukuti sagona mnyumba, ndiye amakagona kuti? Ukapanda kusamala naye ameneyo akugwetsa mmavuto aakulu-ndikunenatu matenda oopsa, kuphatikizapo HIV/Edzi. Ngati wayamba kale kunena kuti ukakanena kwa ankhoswe banja lithapo ndiye kuti iye za banja alibe nazo ntchito koma kusangalatsa chilakolako cha thupi lake basi. Ndiye usazengerezepo apa, pita kaitule nkhaniyi kwa ankhoswe, umve zimene anene. Ngati akufuna kuti banjali lithe, lithe basi. Mwamuna wachimasomaso ndi woopsa kwambiri ndipo safunika kumusekerera. +Asinganga akuti akonza zionetsero Asinganga mdziko muno akonza zionetsero zokhumudwa ndi chigamulo cha bwalo lalikulu la Mzuzu chopereka chiletso kuti asiye kugwira ntchito yawo powaganizira kuti ndiwo akukolezera mchitidwe wosowetsa ndi kupha anthu achialubino. +Mkulu wa bungwe la asinganga mu Afrika la Traditional Medicine Council of Africa (TMCA), Steve Chester Katsonga, watsimikiza kuti zionetserozi zichitika sabata ikudzayi mumzinda wa Lilongwe. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Katsonga: Sitibwerera mmbuyo Polankhula ndi Tamvani Lachitatu, Katsonga adati akonza zionetserozi pofuna kukapereka madandaulo awo kwa mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, kuti apitirize kugwira ntchito yawo mopanda mantha. +Iye wati akonza kuti boma lililonse litumize asinganga 15 ndipo onse akakumana ku Lilongwe komwe akapereke madandaulo awo kuofesi ya Pulezidenti ndi Kabineti. +Bwalo lalikulu la milandu sabata yatha lidapereka chiletso choletsa asinganga mdziko muno koma lidati anthu amene adatenga chiletsocho akuyenera kulengezetsa uthenga woletsa asingangawo kwa masiku 7 mnyuzipepala ziwiri zodziwika ndi nyumba ziwirinso zoulutsa mawu zomwe zili ndi omvera ochuluka. +Mpaka pano uthengawo sudayambebe kulengezedwa monga bwalo lidanenera ndipo loya wa anthu amene adatenga chiletsocho, George Kadzipatike, wati ndalama ndi zomwe zawavuta. +Anthu amene ndikuwaimirira alibe ndalama. Pakufunika pafupifupi K10 miliyoni kuti tilengezere uthengawo, koma tili ndi chikhulupiriro kuti ndalamazi zipezeka ndipo tilengeza momwe khoti lagamulira mpaka asingangawa ataletsedwa ntchito yawo, adatero Kadzipatike. +Komabe Katsonga wati pamene akuluakuluwa akuyanganga ndalama, iwo agwirizana kuti achite zionetsero zamtendere pofuna kuti asaletsedwe kugwira ntchito yawo. +Mutaonetsetsa, ndondomeko yonseyi sidayende mwadongosolo lake. Angotiganizira kuti tikukhudzidwa ndi kuphedwa kwa maalubino koma palibe umboni kuti zili choncho. +Komanso mutha kuona kuti, pakakhala madandaulo pa zomwe mwana wachita, umayenera upeze kholo kuti likambirane ndi mwanayo. Asinganga mdziko muno ali ndi mabungwe, koma tikudabwa kuti ife sanatidandaulire koma adangopita kukhoti kukatenga chiletso, adatero Katsonga. +Adapitiriza kunena kuti: Anthu akupezeka ndi ziwalo, kodi amenewo ndi asinganga? Komanso kodi anthuwo adawafunsa amene wawatuma? Ngati aulula munthu amene wawatuma, bwanji osamumanga munthuyo? Pali zambiri zoyenera kutsatidwa ngati dziko tisanabwere ndi ganizo loletsa asinganga. Nafenso tikufuna kuthandiza dziko kuti mchitidwe wopha maalubino utheretu. +Pokambapo nkhani za zionetsero, Katsonga adati akukhulupirira kuti Mutharika ndiye angathandize pa madandaulo awo chifukwa zikalata zomwe ali nazo kuti azigwira ntchito mdziko muno, zidasaniyidwa ndi mtsogoleri wakale wa dziko lino. +Adati iye: Bungwe lathu kuti likhazikitsidwe udali mgwirizano wa dziko ndi ifeyo asinganga. Kamuzu Banda ndiye adasayinira. Izi zikutanthauza kuti mtsogoleri wa dziko lino ndiye angatithandize. +Ngati mtsogoleri wa dziko angavomereze asinganga, ndiye muganiza kuti nzolondola wina kukangotenga chiletso kuwaletsa? Nanga mabungwe ovomerezeka a asingawa azitani? Kuphedwa mwachisawawa kwa malubino mdziko muno, kwachititsa kuti anthu ayambe kuperekera maganizo kuti opha anthuwa nawonso aziphedwa. +Mwa iwo ndi phungu wa Nyumba ya Malamulo ku Mulanje South, Bon Kalindo, amene wati ngati izi sizichitika, iye ayenda chibadwire kusonyeza kukwiya kwake. +Winanso ndi mtsogoleri wa chipani cha Petra Kamuzu Chibambo, yemwe Lachitatu adauza wayilesi ya Zodiak kuti lamulo loti opha anzawo nawo aziphedwa lilipobe mdziko muno ndipo nkofunika kuti ligwire ntchito pofuna kuteteza miyoyo ya maalubino. +Koma lipoti lomwe latulutsa bungwe loteteza maufulu a anthu padziko lapansi la Amnesty International (AI) lati silingakhale yankho kuti wopha alubino aziphedwanso. +Monga Amnesty International, tikutsutsa kwathunthu ganizo lomapha anthu amene akhudzidwa ndi kuphedwa kapena kuzembetsedwa kwa maalubino. Izi ndi nkhanza chifukwa palibe umboni weniweni kuti chilangochi chingathetse nkhanazi, adatero Deprose Muchena, mkulu wa bungweli kudera la kummwera kwa Afrika (Southern Africa) atabwera kudzacheza mdziko muno masiku apitawa. +Chimanga chikololedwa chochepaUnduna Kauniuni woyamba wa zokolola wasonyeza kuti chaka chino Amalawi akolola chimanga chocheperako kusiyana ndi chaka chatha, chikalata chimene unduna wa malimidwe watulutsa chatero. +Chaka chilichonse undunawu umachita kauniuni katatu pa mbewu, ziweto ndi nsomba pofuna kuunikira kuti zokolola zikhala zotani. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kauniuni woyambayo wasonyeza kuti chaka chino mlingo wa chimanga utsika kuchoka pa matani 2 776 277 chaka chatha kufika pa 2 719 425, ndipo izi zikutanthauza kuti pa makilogalamu 100 alionse omwe tidapeza chaka chatha, chaka chino pazichoka makilogalamu awiri. +Kauniyu wapezanso kuti fodya wa chaka chino achuluka kuchoka pa makilogalamu 192 967 541 chaka chatha kufika pa makilogalamu 211 083 000 chaka chino pomwe thonje atsika ndi makilogalamu 43.2 pa makilogalamu 100 alionse omwe adakololedwa chaka chatha. +Undunawu wati mpunga uchuluka ndi makilogalamu 1.4 pa makilogalamu 100 omwe adakololedwa chaka chatha pomwe mtedza uchuluka ndi makilogalamu 4.5, nyemba 5.2 ndipo nandolo 3.1 pa makilogalamu 100 aliwonse omwe adakololedwa chaka chatha. +Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a zaulimi wa Civil Society Agriculture Network (Cisanet) Tamani Mvula Nkhono adati kauniuni wa mtunduwu ndiwofunika chifukwa umapereka chithunzithunzi cha kakololedwe. +Iye adati undunawu wachita bwino kutulutsa zotsatira zakauniuni woyambayu koma lipitirize kuunikanso kawiri kamene katsala. +Mike Mkwate: Chilombo pakati pa Bullets Dzina la Mike Mkwate si lachilendonso mdziko muno malinga ndi ntchito yomwe akuphika ku Nyasa Big Bullets. Wasewera magemu awiri mu TNM amene adayamba mpaka kumaliza ndipo magemuwo adasankhidwa kukhala Man-Of-Match. Kusewera kwake kukupatsa chidwi anthu ambiri. BOBBY KABANGO adacheza naye kuti amve zambiri za iye motere: Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mkwate kunyadira kachikho ka man-of-the-match Zabwinobwino mnyamata? Bhobho, amwene! Kodi Mike Mkwate ndani? Ineyo ndiye Mike Mkwate, mwana wa ku Balaka koma ndikukhala ku BCA Hill ndi makolo anga mumzinda wa Blantyre. Ndili ndi zaka 20, woyamba kubadwa mwa ana awiri. +Kusukulu udapitako? Pangono, amwene, ndidayambira sukulu pa Bangwe pulaimale, ndamalizira pa Matindi fomu 4 koma sindidakhoze bwino moti chaka chamawa ndibwerezanso. Ndikufuna ndikhoze bwino chifukwa ndili ndi lingaliro lopanga kosi ya unamwino (Nursing). Ndimafuna nditamadzasewera mpira koma ndikugwiranso ntchito. +Mpira udayamba liti? Ndidayamba ndili wamngono kupulaimale. Zenizeni zidaoneka ndili fomu 2 ndikusewera ku Surestream. +Udalingalira kuti udzasewera ku Bullets? Ayi. Moti tsiku loyamba kusewerera Bullets ndidali ndi mantha, ndimati ndikaona masapota aja ndiye ulakwitsenso, eeh! Ndidali ndi mantha, komabe anzanga amandilimbikitsa ndipo lero zikutheka, mantha adandichoka. +Ndi kangati udasankhidwa man-of-the-match? Ndasankhidwapo kawiri. Ku Bullets ndasewera magemu 6 muligi koma awiri okha ndi amene ndidayamba mpaka kumaliza moti awiriwo ndidasankhidwa kuti ndasewera bwino. Magemu enawo ndimachokera panja. Ndikusewera mu Wizards ndidasankhidwanso kukhala man-of the-match maulendo 7. +Ndiwe Msilamu, kodi namazani simakusokonezani maseweredwe? Osati kwambiri koma munthu ndi munthu, ngati sunadye umamva njala ndiye zimandikhudza inde, koma osati kwambiri. +Henry Mussa: Akusowa tulo ndi Teba Anthu omwe adagwirako ntchito mmigodi ya mdziko la South Afrika pamgwirizano wa Temporary Employment Bureau of Africa (Teba) kapena kuti Joweni akhala akudandaula kwa nthawi yaitali pankhani yokhudza ndalama zawo za penshoni. Sabata zingapo zapitazi nduna ya zantchito Henry Musa idapereka chiyembekezo mmitima ya anthu odandaulawa powauza kuti boma la Malawi ndi South Africa ali kumapeto kwa zokambirana pankhaniyi kuti anthuwa alandire ndalama zawo. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere: Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Tadzifotokozeni mwachidule, olemekezeka. +Ine ndine Henry Mussa, phungu wa dera la kummawa kwa boma la Chiladzulu, komanso ndine nduna ya zantchito ndi kuphunzitsa anthu ntchito. +Mussa: Nkhani ya Teba sikutigona nayo Pali gulu la anthu omwe adapita kukagwira ntchito mdiko la South Afrika pamgwirizano wa Teba omwe mpaka pano akuti sadalandirebe ndalama zawo za penshoni. Inu ngati nduna ya zatchito mukudziwaponji? Nzoonadi anthu amenewa sadalandire ndalama zawo koma akhulupirire kuti ifeyo sitikugona chifukwa cha nkhani yomweyi. Tili kalikiriki kukambirana ndi dziko la South Afrika kuti anthu amenewa athandizike basi chifukwa ndalamazo ndi zawo osati za munthu wina kapena kuti akupemphetsa, ayi. +Komanso tamva kuti maina ena akusowa mkaundula kodi pamenepa zikukhala bwanji? Nzoona pamaina 36 875 omwe adaperekedwa ku South Afrika, maina 9 440 okha ndiwo adapezeka mmakina a kompyuta, kutanthauza kuti maina 23 427 akusowa. +Mainawa akusowa chifukwa chiyani? Inde, tidafufuza nanga unduna ukulukulu ngati uno ungangokhala chete pankhani yaikulu ngati imeneyi? Pali zifukwa zingapo. Choyamba, anthu ena amalakwitsa maina ndi manambala a pachiphaso polemba, nanga mmesa akhala nthawi yaitali. Chachiwiri, anthu ena panthawiyo amachita chodinda chala kaamba kosatha kulemba koma adamwalira ndiye amasayinira chikalata chawo ndi abale awo, zomwe zidachititsa kuti asakapezeke mmakina kumeneko. +Ndiye ngati unduna, anthu oterowo muwathandiza motani? Tidakambirana kale ndi dziko la South Afrika kuti aunikenso moti ndikunena pano anthuwo akusayinanso makalata ena kuti titumize ku South Afrika. +Zaka 18 kwa mphunzitsi wochimwitsa mwana Mphunzitsi yemwe adachimwitsa mtsikana wasukulu wa zaka zosadutsa 16 komanso kumupatsa mankhwala ochotsera pathupi wapukusa mutu wopanda nyanga bwalo la milandu la majisitireti ku Mzuzu litagamula kuti akalangidwe kundende kwa zaka 18. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Apa nkutitu mbwaloli muli ziii pomwe majisitireti Gladys Gondwe amapereka chigamulo chake kwa Mtendere Phiri, wa zaka 31, wochokera ku Bembeke, T/A Kachindamoto mboma la Dedza, yemwe amaphunzitsa pasukulu ina ya pulaimale ku Ekwendeni mboma la Mzimba. +Zidaonekeratu kuti mphunzitsiyu sadali wokonzeka kuti alandira chigamulo cha mtunduwu chifukwa majisitiretiyu asadafike mbwaloli, Phiri adamveka akufunsa apolisi omwe adali kumuyanganira ngati zingatheke kutuluka patsikuli. +Apolisiwo adamuyankha momupatsa chikhulupiriro chonse kuti zikuoneka kuti zimuyendera ndipo akonzeke chifukwa patsikuli akagona pofewa kunyumba. +Komatu zinthu sizidamuyendere chifukwa mmphindi zisanu zokha, majisitireti adali atapereka chigamulochi. Phiri adangoti zyoli mchitokosi cha bwaloli. +Popereka chigamulo chake Lolemba, Gondwe adati Phiri akuyenera kuseweza zaka 16 ndi kugwira ntchito yakalavula gaga pogona ndi mtsikana wosakwana zaka 16, ndipo pamlandu wopereka mankhwala ochotsetsa mimba adampatsa zaka ziwiri zomwe ziyendere limodzi ndi za mlandu woyambawu. +Iye adati wapereka chilango chokhwimachi pofuna kupereka phunziro kwa aphunzitsi ena omwe ali ndi khalidwe logonana ndi ana awo asukulu mmalo mowalimbikitsa pamaphunziro awo. +Mtumiki wa Mulungu adalosera Onse okhulupirira amadziwa kuti zodzera mmanja mwa Mulungu nzodalitsika ndipo zimayenda moyera monga momwe zikuyendera pakati pa mthutha wa chikopa Elvis Kafoteka ndi Thokozani Mazunda. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Awiriwa akuti adakumana mchaka cha 2012 kumapemphero kutchalitchi cha Revival Church of All Nations ku Ntcheu, koma nkuti mneneri wa Mulungu kumeneko, Themba Jere, atalosera kale kuti chisadafike chaka cha 2016, Thoko adzakhala atakumana ndi wachikondi wake. +Elvis akuti awiriwa atakumana mu 2012, adayamba kucheza ngati munthu ndi mnzake, osaganizirana kuti maganizo a wina ngotani, kufikira mu December mchaka cha 2015 pomwe iye adafunsira namwaliyo. +Thokozani ndi Elvis patsiku la chinkhonswe Mmene tinkakumana tidali tisakudziwana koma tidakhulupirira kuti mphamvu ya Mulungu idalipo chifukwa tidayamba kucheza ngati anthu oti tidadziwana kalekale. Tidapitiriza choncho mpaka 2015 pomwe ndidamufunsira ndipo adandivomera, adatero Elvis. +Iye akuti panthawi yonseyi, Thoko ankamubisira za masomphenya a mneneri Jere ndipo pa 31 December 2015 kuti mawa lakelo ndi 2016, awiriwa adakumana kumapemphero a usiku komwe adafunsirana. +Mwina samandiuzira dala kuti aone zotsatira za masomphenya a mneneriyo. Patsikulo kudali kuti mawa lake 2016 wafika ndipo ndimakhulupirira kuti mphamvu ya Mulungu idagwirapo ntchito kwambiri, adatero Elvis. +Pa 4 June awiriwa adapanga chinkhoswe kunyumba kwa a Loga mboma la Ntheu ndipo pologalamu yaukwati idakonzedwa kuti udzakhaleko pa 3 June chaka chamawachi. +Iye adati amakonda chilichonse pamoyo wa Thoko monga momwe naye Thoko akuti amakondera Elvis. +Anatchezera Ndazunguzika Agogo, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndine mtsikana wa zaka 18 ndipo ndinazunguzika mutu chaka chatha pomwe ndinapezeka ndi kachilombo ka HIVkoma sindinagonepo ndi munthu ngakhale ndinali nacho chibwenzi. Amayi anga ali ndi HIV koma abambo anga alibe. Banja la makolo anga lidatha ndili ndi chaka ndi miyezi isanu ndi iwiri. Ndine woyamba kubadwa koma ana onse obadwa kwa amayi anga amabadwa ndi kachilombo. Amayi anga akuti adatenganso pathupi ine ndili ndi miyezi 9 koma abambo anga amakana kuti mwanayo adali wawo. Ndiye ine zinandizunguza mutu kuti kodi zidayenda bwanji. Abambo anga ndi amayi anga ondipeza amandinena kuti ndinatenga kachilomboka kwa chibwenzi chomwe ndinali nacho. Mankhwala ndinayamba kumwa sabata yomwe anandipeza ndi kachilomboka popeza chitetezo chinali chotsika kwambiri, koma sindinadwale, ndidangopita ndekhala kukayezetsa ndipo ndinalibe nkhawa iliyonse. Koma pano ndikusowa mtendere. Ndithandizeni, chonde, nditani? RM, Mzuzu Zikomo mwana wanga RM, Nkhani yako ndaimva bwino lomwe ndipo ndakunyadira chifukwa ndiwe mtsikana wolimba mtima. Si ambiri amene amalimba mtima kukayezetsa magazi ngakhale sakudwala kuti adziwe momwe chitetezo chilili mthupi mwawo, ambiri amaopera kutalitalisafuna kudziwa nkomwe ngati ali ndi kachilombo kapena ayi. Wanena kuti udapezeka ndi kachilombo ka HIV chaka chatha koma wanenetsa kuti sudagonanepo ndi munthu wina aliyense ndiye zidatheka bwanji kupezeka ndi kachilomboka? Iyidi ndi nkhani yozunguza chifukwa ngakhale pali njira zambiri zotengera kachilomboka, njira yodziwika kwambiri ndi yogonana mosadziteteza ndi munthu amene ali ndi kachilomboko. Koma zimatheka ndithu kutenga kachilomboka mwatsoka ndithu ndipo imodzi mwa njira zotere ndi kutengera kachilomboka pobadwa kuchokera kwa mayi amene ali nako. Ndikhulupirira iweyo udatenga kachilomboka panthawi yobadwa chifukwa wanena kuti ana onse obadwa mwa mayi ako akumapezeka ndi kachilombo ka HIV. Chomwe ndingakulangize nchoti pitiriza kumwa mankhwala otalikitsa moyo ndipo udzisunge monga wadzisungira nthawi yonseyi ndipo udzakhala ndi moyo wautali, wosadwaladwala. Uziyesetsa kuti usamakhale ndi nkhawa chifukwa izi zikhoza kubweretsa mavuto ena pamoyo wako. Uzilandira uphungu woyenera kwa akatswiri odziwa za kachilombo ka HIV kuti ukhalebe ndi moyo wathanzi ndi wansangala, osati kudzimvera chisoni. Kupezeka ndi kachilombo sikutanthauza kuti ufa nthawi iliyonse, ayi, utha kukhala zakazaka mpaka kukalamba monga ine, bola kudzisamalira. +Amadikira ndimuimbire Anatchereza, Ndine mtsikana wa zaka 15 ndipo ndili ndi chibwenzi koma anapita ku Nkhotakota. Poyamba timaimbirana foni koma panopa adaleka, amadikira ine ndiimbe. Kodi pamenepa ndimudikire? Agogo, ndithandizeni. +Aphangirana ufa Mwambo wa mapemphero Achisilamu otchedwa dawa udasokonekera kwa Chitulu kwa T/A Mwambo mboma la Zomba Loweruka pa 2 April pomwe khwimbi la anthu lidakhamukira kumeneko kukalimbirana ufa womwe amati agawe mwambowo ukatha. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kuderalo kudafika bungwe la Eid Charitable la mdziko la Qatar lomwe limachititsa mapemphero Achisilamu ndipo pakutha pa mapemphero amayenera kugawa ufa kwa Asilamu ndi anthu ena ovutika. +Asanayambe kugawa chakudyacho amayamba ndi mapemphero a dawa ndi kupereka mwayi kwa ofuna kulowa Chisilamu kuti atha kutero povomereza kuti Muhammad ndiye mneneri wa Mulungu womaliza. +Mapemphero akupita kumapeto, Asilamuwa adapempha anthu amene ankafuna kulowa Chisilamu kuti anene pemphero loti Ashihadu anla ilaha llah. Wa a shadu anna Muhammad u rrasulu llah (Ndikuikira umboni kuti pali Mulungu mmodzi yekha. Ndipo ndikuikiranso umboni kuti Muhammad ndi mtumiki wake womaliza). +Khwimbi la anthu kudikira kuti alandire kangachepe Apa mpomwe gulu la anthu ambiri, ena mwa iwo Akhrisitu, adanena nawo pempheroli ndi kuvomereza kuti alowa Chisilamu, adatero Shehe Mustapha Saidi, yemwe amayanganira mzikiti wa Chitulu. +Mwambo wa dawa uli mkati, galimoto yomwe idanyamula ufawo idatulukira, zomwe zidayambitsa kuti khwimbi la anthu likhamukireko ndipo padali ali nmwana agwiritse pomwe amati ayambe kugawa ufawo. +Mwina poona kuti suwakwana onse, zidavuta kuti akhale pamzere ndipo ena adayamba kukwera okha pamwamba pa loleyo kukadzithandiza okha potenga matumba a ufa. Ena amatenga awiri ena atatu amene, olemera makilogalamu 25 limodzi. +Martin Umi, wa mmudzi mwa Chitulo, akuti iye ndi Mkhristu koma adalumbira nawo ponena pemphero la Chisilamulo kuti alandire nawo ufa. +Kunena zoona ndidavomereza kuti ndalowa Chisilamu koma ndimangofuna kuti ndilandire nawo ufawo chifukwa cha njala pakhomo panga. Komabe mwina mtsogolomu ndilowadi Chisilamu, nanga si anthu amene akutithandiza, adatero Umi. +Iye adati adakwanitsa kutenga matumba awiri, koma adavulala atapondedwa pamene amathawitsa ufawo. +Mfumu Chitulu idati kudera lake komanso madera ena kuli njala yadzaoneni chifukwa mvula idasiya kugwa mu January kupangitsa kuti chimanga chipserere. +Momwe njala yavutira kuno, nkovuta kuti wina angatsale pakhomo atamva kuti kwina kukubwera chakudya. Si zodabwitsa kuona kuti anthu adaphangirana ufawo, idatero mfumuyi, yomwe mmudzi mwake muli anthu 1 470, omwe ndi mabanja 240. +Shehe Saidi adati chipwirikiticho chidakhumudwitsa mamembala awo amene sadalandireko ufawo. +Zachisoni kuti mamembala athu ambiri sadalandire nawo ufawo, zomwe zachititsa kuti ena asiye kutumiza ana awo kumadrasa [sukulu ya ana ophunzira Chisilamu], adatero Saidi, yemwe adati akuyembezabe kuona ngati omwe amati alowa Chisilamu patsiku logawa ufalo abwere kumzikiti kudzapemphera. +Si bwino kunamizira kulowa mpingo kaamba koti ukufuna chithandizo cha kuthupi koma uzilowa mpingo kaamba kofuna kukapulumuka kumwamba, adaonjezera Shehe Saidi, pouza Msangulutso Lachisanu lapitali. +Lero Lachisanu olo mmodzi mwa omwe adati alowa Chisilamu patsikulo palibe amene wabwera kumapemphero. Amatero? Bungwe la Eid Charitable lidabweretsa ufa mdziko muno womwe udagawidwa mboma la Zomba, Machinga ndi Mangochi. +Mkulu wa gululi, Ali Muhammad Al-saaq, adati adauzidwa ndi bungwe la Zamzam Foundation la ku Malawi za mavuto amene Amalawi akukumana nawo kaamba ka njala. +Titamva za mavutowa, tidabwera ndi ufa kuti ovutika athandizike. Tipemphenso anthu ena kuti athandize dziko lino. Ifeyo tikabwerera tikasakanso thandizo lina ndipo tipitiriza kuthandiza dziko lino, adatero Al-saaq. +Asinganga asowa mtengo wogwira Chigamulo cha bwalo lalikulu ku Mzuzu kuletsa asinganga kuti asagwirenso ntchito mdziko muno zabweretsa mpungwepungwe ndipo asinganga eniake akuti sakumvetsa chomwe bwaloli likutanthauza. +Escom in free-for-all fuel scam Wait gets longer Secrecy over party funders Lachitatu bwaloli lidapereka chiletso kwa asinganga kuti asagwirenso ntchito mdziko muno ponena kuti ndizo zikukolezera kuphedwa kwa maalubino. +Chiletsocho chakhudzanso manyuzipepala ndi nyumba zoulutsa mawu kuti asiye kufalitsa ndi kuulutsa mauthenga a malonda a asingangawa poti nazonso zikukolezera mchitidwewu. +Loya wa odandaula: Kadzipatike Chidatsitsa dzaye ndi nkhani yomwe amuna awiri ndi mayi mmodzi a mumzinda wa Mzuzu ataitengera kubwalo lalikululo komwe adakamangalira asinganga Masamba Asiyana Mwale ndi Apite Apitana Chiwaya komanso nganga zina zogulitsa mankhwala azitsamba ndi kuchita maula kapena zamatsenga ponena kuti anthuwa adawakwangwanula mnjira zosiyanasiyana. +Anthuwa ndi Evans Mponda, Osward Phiri ndi Mary Nyirenda. +Mponda adauza khoti kuti sadachire kumatenda ake atapempha chithandizo cha mankhwala kwa Mwale ngakhale adalipira ndalama zokwana K120 000 atakopedwa ndi zomwe adawerenga munyuzi kuti singangayo atha kuthetsa vuto lake. +Naye Phiri adati ali ndi msuwani wake wa zaka 9 ndipo ali ndi nkhawa kuti atha kuphedwa kaamba ka zomwe zakhala zikuwaonekera anthu achialubino masiku ano ndi mmbuyomu; pomwe Nyirenda adati Chiwaya adamulonjeza kuti katundu wake amene adabedwa apezeka komanso kuti mwamuna wake amene adamuthawa ukwati abwerera pasanathe sabata, zomwe sizidachitike chonsecho atalipira ndalama zokwana K50 000. +Koma chiletso cha khoti kwa asinganga onse mdziko muno sichidakomere mkulu wa bungwe la asinganga la Traditional Healers, Edward Kayange. +Ngati pena zalakwika, ndi bwino kukambirana kuti mupeze yankho. Koma zonse zikulankhulidwazi, ife sitikudziwapo kanthu. +Kodi kuthandiza munthu amene watipeza ndi vuto palakwika? Ndife odabwa ndi chiletsochi, adatero Kayange, koma sadafotokoze chomwe bungwe lawo lichite. +Woweruza milandu amene adapereka chiletsocho, Dingwiswayo Madise, adati ngati wina ayerekeze kutsutsana ndi chiletso cha bwalolo, ndiye kuti akuyenera kudzayankha mlandu. +Pakalipano, loya wa omwe adakamangamala kukhoti lalikulu, George Kadzipatike, wati alengeza za chiletsochi mnyuzi ziwiri zomwe zili ndi awerengi ambiri komanso mnyumba zoulutsira mawu ziwirinso zomwe anthu amakonda kumvera kuti nganga zonse mdziko muno zidziwitsidwe za chigamulo cha bwalochi. +Wa ku Mangalande anjatidwa atagwiririra wa ku Amerika Bwalo la Chief Resident Magistrate ku Lilongwe lagamula nzika ya dziko la ku Britain Amrish Magecha kukaseweza zaka 8 mundende chifukwa chogwiririra nzika ya ku Amereka. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kalata ya chigamulo chomwe chidaperekedwa pa 6 May, 2016 ndi Chief Resident Magistrate Ruth Chinangwa chasonyeza kuti nzika za maiko awiriwa zidakumana kumalo achisangalalo komwe zidamwa zakumwa zoledzeretsa. +Wodandaula adauza bwalo kuti Magecha adamutengera kumalo ogona alendo otchedwa Pine Lodge mumzinda wa Lilongwe usiku wa pa 8 August, 2015 komwe adamulowetsa mchipinda nkukhoma chitseko kenako nkumugwiririra. +Atakhoma chitseko ndidadzadza ndi mantha ndipo nditamupempha kuti atsegule adakana kenako nkuyamba kundivula mogwiritsa ntchito mphamvu. Tidalimbana kwa kanthawi koma kenako mphamvu zidandithera mpomwe adapeza danga nkundigwiririra, adatero wodandaula. +Mugecha adavomera kuti adagonana ndi wodandaulayo koma adati zonse zidali zochita kupangana osati kugwiririra monga mmene adanenera. +Tidatengana nkupita mchipinda ndipo ine ndidakhoma chitseko pomwe iye adafikira kukhala pabedi kenako nkuvula nsapato nkugona. Nditakhala pamphepete pake, tidayamba kugwiranagwirana kenako adandiuza kuti ndivale kondomu. +Ndidavomera ndipo nditavala tidayamba kugonana. Titamaliza ndidakataya kondomuyo nkudzagona ndipo iye adandiuza kuti akufunika akapezeke kuntchito 7 koloko mmawa. Kutacha ndidakamutula komwe amagona ku Crown Lodge, adatero Mugecha. +Koma patsiku loyambirira kuwonekera kukhoti, Mugecha adati: Mundikhululukire pa zomwe zidachitika Ndikupepesa kumtundu wa Amerika pazomwe ndidachita. Ndine nzika ya ku Mangalande ndipo ndikufuna kazembe wa Mangalande adziwe zimenezi. Ndidakwatira zaka 19 zapitazo ndipo ndili ndi mwana mmodzi. +Youth Week ibwereredi Achinyamata, mafumu Mtsogoleri wa achinyamata pa ndale wa bungwe la Young Politicians Union Clement Mukuwa wati ndi wosangalala ndi ganizo la boma lofuna kukhazikitsanso sabata ya achinyamata (Youth Week) chifukwa likugwirizana ndi zomwe achinyata adaika pamndandanda wa zolinga zawo. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Tili ndi mndandanda wa zomwe tikufuna achinyamata atamachita ndipo chimodzi mwa izo ndi kugwira ntchito modzipereka ndiye tikakumbuka zomwe Youth Week inkachita, zikugwirizana ndi mfundo imeneyi, adatero Mukuwa. +Kudikira kuti boma likonze: Munthu kuoloka movutikira paulalo woonongeka Phungu wa kumpoto cha kummawa kwa boma la Mchinji, Alex Chitete, ndiye adayambitsa nkhaniyi mNyumba ya Malamulo pomwe aphungu amaunika momwe chuma cha dziko chayendera pamiyezi isanu ndi umodzo (6). +Phunguyu adapempha boma kuti likhazikitsenso sabata ya achinyamata monga zidalili mnthawi ya ulamuliro wa malemu Dr. Hastings Kamuzu Banda pomwe achinyamata mdziko muno adali ndi sabata yogwira ntchito zachitukuko mmadera awo pofuna kuwaphunzitsa za ubwino wogwira ntchito modzipereka potukula dziko lawo. +Iye adati panthawi ya ulamuliro wa chipani chimodzi achinyamata ankatenga gawo lalikulu pachitukuko kusiyana ndi masiku ano pomwe kuli ntchito zogwira ndi chiyembekezo cholandira dipo yomwe akugwira ndi anthu akukuluakulu. +Poyankhapo, nduna ya zantchito Henry Mussa adati ganizoli si loipa koma silokakamiza ndipo mmapulani a boma muli kale ndondomeko zomwe akuti achinyamata azipatsidwa mpata kutenga nawo mbali pantchito zina. +Iye adati mundondomekoyi, ntchito zina zomwe zizigwiridwa ndi zachitukuko monga momwe zinkakhalira mnyengo ya Youth Week kalelo. +Tidayankha kale pankhani imeneyo kuti si zokakamiza koma ndondomeko ilipo kale moti pompanopompano ziyambika, adatero Mussa. +Mukuwa adati ngati mtsogoleri wa achinyamata pandale akhoza kukhala wokondwa anthu atadziwitsidwa ubwino wa Youth Week ndi zolinga zake kuti mtima wogwira ntchito wodzithandiza posayembekezera malipiro ubwerere mwa Amalawi. +Katswiri pa mbiri ya dziko lino, Desmond Dudwa Phiri (DD Phiri), ndi mafumu angapo akuluakulu ati ganizo lokhazikitsanso sabata ya achinyamatali ndi lofunika kwambiri pachitukuko cha dziko la Malawi. +DD Phiri adati Youth Week ndi nyengo yomwe achinyamata ankatengapo mbali pachitukuko chosiyanasiyana ngati nzika za dziko mwaulere ndipo izi zinkathandiza kutula midzi ndi madera omwe ankakhala. +Nthawi imeneyi achinyamata ankakhala otangwanika kwambiri pantchito zachitukuko monga kukonza misewu, milatho, zipatala, sukulu ndi zina mmadera mwawo mwaulere ndipo zinthu zinkayenda, adatero mkhalakaleyu. +Iye adati ntchito ngati zomwezi, pano zimalira bajeti yaikulu kuti anthu agwire, mapeto ake ndalama zikasowa, zitukukozi zimayamba zaima kwa nthawi yaitali, zinthu nkumapitirira kuonongeka. +Youth Week inkakhalako chaka chilichonse nyengo ngati ino ya Pasaka ndipo tinkadziwiratu kuti misewu yonse yoonongeka, milatho, zipatala, sukulu ndi nyumba za aphunzitsi zomwe zikuonongeka zikonzedwa. +Pano ntchito ngati zimenezi zimalinda ndalama za mbajeti kuti anthu kapena makontirakitala azigwire. Ngati ndalamazo palibe, ndiye kuti zinthuzo zizingopitirira kuonongeka mpaka ndalama zidzapezeke, adatero DD Phiri. +Mkuluyu adati Youth Week idatha mdziko muno mutabwera ulamuliro wa zipani zambiri poganiza kuti idali nkhanza kwa anthu (thangata) ndipo mmalo mwake boma lidasenza lokha udindo wogwira ntchito zachitukuko. +Iye adati koma anthu sankaona Youth Week ngati thangata ndipo ankagwira ntchito modzipereka ndi umodzi mpaka pomwe adauzidwa kuti ndi thangata. +Mkulu wodziwa za mbiri yakaleyu adati maiko ambiri omwe ndi otukuka pano adayamba ndi eni ake kudzithandiza ndipo boma linkangobwera pambuyo kudzawonjezera pomwe paperewera. +Mfumu yaikulu (T/A) Maseya wa ku Chikwawa akugwirizananso ndi ganizoli ponena kuti achinyamata amaphunzira ntchito zosiyanasiyana panyengoyi chifukwa amasakanikirana ndipo omwe adali ndi luso amagawira anzawo pogwira ntchitozo. +Iye adati kudzera mnjira imeneyi, achinyamata amakula ndi mtima wokonda ntchito ndiposo zimawathandiza kukhwima mmaganizo kuti paokha akhoza kupanga chinthu chooneka popanda kuyanganiridwa. +Zidali zokoma kwambiri moti zitati zayambiranso zikhoza kukhala bwino kungoti nzofunika kuti poyambitsapo aunike bwinobwino kuti ntchitozo angazigawe motani potengera zaka kuti zisakolane ndi nkhani yogwiritsa ana ntchito yoposa msinkhu wawo, adatero Maseya. +Inkosi Chindi ya ku Mzimba idasangalalanso ndi ganizoli ponena kuti nyumba zambiri zophunziriramo, zokhalamo aphunzitsi, milatho ndi misewu zomwe pano zili ngati bwinja zikhoza kukonzedwa mosavuta. +Chitukuko cha kudera ndi udindo wa anthu okhala kudera limenelo ndiye anthu atafotokozeredwa bwinobwino phindu lomwe angapeze kuchoka muntchito zachitukuko cha Youth Week, sindikukhulupirira kuti angawiringule, adatero Chindi. +Iye adati munyengoyi, achinyamata amagwira ntchito zosiyanasiyana monga kulambula misewu, kukonza milatho, nyumba za aphunzitsi ndi zitukuko zina uku akutayitsa nthawi ndi macheza. +Naye T/A Mkanda ya mboma la Mchinji idati ana ambiri masiku ano amalephera kupita kusukulu nyengo ya mvula kaamba kolephera kuoloka mitsinje chifukwa chodikirira kuti boma likonze milatho. +Kudali kukwaya ku Mtima Woyera Udali ulendo wokhetsa thukuta lowopsa kuti zonse zilongosoke pakati pa Gray Lizimba ndi Iness Chimombo koma zonse zidafika pampondachimera Loweruka lapitali pomwe awiriwa adapatsana malonjezano omaliza. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Inde, pamtendere ndi pamavuto, moyo wabwino kapena matenda sadzasiyana. Awa ndiwo adali malonjezo pakati pa Gray ndi Iness omwe amachokera ku Bembeke mboma la Dedza ndipo onse amachita bizinesi mumzinda wa Lilongwe komanso amayimbira limodzi kwaya ku Mtima Woyera Parish ya mpingo wa Katolika mumzinda wa Lilongwe. +Gray akuti ulendo udayamba mchaka cha 2009 awiriwa atakumana kutchalitchi ndipo Gray sadafune kuchedwa koma kufunsira pomwepo koma akuti sizidayende. +Adandiyankha kuti ndisadzayerekeze kumulankhulanso za nkhaniyo, koma sindikadakwanitsa kutero. Mtima wanga udali pa iye ndipo ndidapitiriza kutchetcherera mpaka mu April, 2012 mpomwe adandilola, adatero Gray. +Gray ndi Iness kupsopsonana patsikulo Iye adati atangomva mawu oti ndavomera adamva ngati wanyamula dziko lonse mmanja mwake, mtima ukudumphadumpha uku mmasaya muli chimwemwe chokhachokha. +Iye akuti adakhala pachibwenzi mpaka mchaka cha 2014 mwezi wa November pomwe awiriwa adapanga malonjezano oyamba pachinkhonswe ndipo adagwirizana kukhala zaka zina ziwiri asadapange ukwati kuti akonzekere mokwanira. +Kuchoka apo tinkakonzekera ukwati wathu ndipo tonse tidaikapo mtima mpakana zonse zidatheka pa 4 June, 2016. Tidakadalitsira ku Mtima Woyera ndipo madyerero adali kubwalo la St Peters Anglican ku Lilongwe, adatero Gray. +Iye akuti Iness ndi chimwemwe komanso ufulu wake chifukwa amamulimbikitsa mzinthu zambiri ndi kumuthandiza mmaganizo pomwe mutu waima. +Iness sadafune kunena zambiri koma kungotsimikiza kuti iye ali ndi chimwemswe kuti mtunda womwe adauyamba zaka 7 zapitazo wafika pampondachimera. +Timakakonza za ntchito Wakaona nyanja adakaona ndi mvuwu zomwe. Mauwa apherezedwa ndi ukwati wa Amos Mazinga wa ku Dowa mmudzi mwa Ngozi, T/A Chiwere, ndi Regina Mkonda wa mmudzi mwa Reuben, mboma la Mulanje. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Awiriwa akuti adakumana kuofesi ya aphunzitsi ku Nathenje mchaka cha 2014 atamaliza maphunziro a zauphunzitsi, komwe akuti amakolongosola za malo omwe azikagwirira ntchito koma ulenje udabzola mlingo ataphana maso. +Amos adati iye atangoonana maso ndi maso ndi Regina, mtima wake udadumpha kwambiri moti adalakalaka zotuluka muofesimo kuti akadzione ngati akukwanira kulankhula donayo. +Amos ndi Regina kupsopsonana patsiku la ukwati wawo Zimene zidandichitikira sizidandichitikileponso mmoyo mwanga. Ine ndi mmodzi mwa anthu omasuka komanso opanda mantha ngakhale pamaso pa anthu, koma tsiku ili lokha ndidaona nyenyezi yothobwa mmaso, adatero Amos. +Iye akuti panthawi yomwe iwo amayembekezera kuthandizidwa mpamene adapeza mwayi womulankhulira msungwanayo ndipo adacheza bwino kwambiri mpakana kupatsana nambala za foni za mmanja. +Kusiyana kwa pamenepo kudali madzulo atalandira thandizo, koma kudali kusiyana pamaso chabe chifukwa macheza awo adapitirira kudzera pafoni. +Tidakhala nthawi yaitali tikuchezerana pafoni mpaka tsiku lina nditalimba mtima ndidayambitsa nkhani yachikondi, koma kunena zoona ndidalimbana naye mpakana adatheka moti lero ndikakhala ndimadziwa kuti nane mpatali, adatero Amos. +Iye akuti chikondi chake pa Regina chidakula kwambiri kaamba ka khalidwe lake lokonda kupemphera, kuchita zinthu mwanzeru ndi modzilemekeza komanso mwansangala. +Regina adati iye poyamba adamutenga Amos ngati mchimwene koma pangonopangono chikondi chidayamba kumugwira moti samafunanso kuti Amos adzagwe mmanja mwa munthu wina koma iye. +Iye adati ngakhale amakanakana poyamba mtima wake udali utalola kale koma amafuna kuona ngati Amos adalidi munthu wachilungamo, wosangofuna kumuseweretsa. +Sindidafune munthu woti kugwa naye mchikondi panthawi yochepa kenako nkukhumudwitsidwa, ndiye ndimayenera kuonetsetsa kuti ndikudzipereka mmanja mwa woyeneradi, adatero Regina. +A Malawi adalimba nazo chaka chatha Ululu, kulavulagaga ndi kupala moto kudalipo mchaka chomwe changothachi monga momwe akadaulo mnthambi zosiyanasiyana akunenera kuti padalibe popumira koma kubanika kokhakokha. +Malinga ndi akadaulo a zamaufulu, zaumoyo ndi oyimira anthu ogula ndi kugwiritsa ntchito zinthu zosiyanasiyana, Amalawi adawawulidwa, makamaka pa mmene ogulitsa zinthu amakwezera mitengo ndi mmene ntchito zina monga zaumoyo, ufulu wa anthu, magetsi ndi madzi zidayendera mchaka changothachi. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Madzi ndi moyo: Mnyamatayu sakadachitira mwina koma kupeza njira yomwera madzi ku Nkhotakota Za umoyo Chaka cha 2015 ndi chaka choyamba chomwe tidaona anthu odwala mchipatala akudya kamodzi patsiku osatengera mtundu ndi kuchuluka kwa makhwala omwe akulandira pavuto lawo. +Chaka chomwechi ndicho kudali chionetsero cha anamwino ndi azamba pa nkhani yoti boma silikuwalemba ntchito ngakhale kuti adachita ndi kumaliza maphunziro awo a ntchitoyi panyengo yomwenso ogwira ntchito zachipatala ali operewera. +Malingana ndi mkulu wa anamwino ndi azamba, Dorothy Ngoma, cholinga cha chionetserochi chidali kupempha boma kuti lilembe ntchito achipatala omwe adamaliza maphunziro komanso libweze ganizo loti anthu odwala azidya kamodzi patsiku. +Iye adatinso nkhani ina yodandaulitsa idali kusowa kwa mankhwala mzipatala, zomwe zidachititsa kuti anthu osauka asakhale ndi mwayi wolandira thandizo loyenera akadwala. +Chomwe ife tikufuna nchakuti anamwino ndi azamba onse omwe sadalembedwe ntchito alembedwe komanso chilinganizo choti anthu odwala azilandira chakudya kamodzi mzipatala chibwezedwe chifukwa munthu wodwala amafunika chakudya chokwanira kuti mankhwala agwire bwino ntchito mthupi, adatero Ngoma. +Mkulu wa bungwe loyanganira za ufulu wa anthu pa nkhani za umoyo, Charles Nyirenda, adati kafukufuku yemwe bungweli lidachita mzipatala zingapo mdziko muno adaonetsa kuti mankhwala mzipatalazi mudalibe. zaumoyo Peter Kumpalume adati mankhwala adasowa mzipatala kaamba ka anthu ena oipa mtima omwe amaba mankhwala nkumakagulitsa posaganizira miyoyo ya anthu. +Ndunayi idalonjeza akuti ithana ndi anthu onse omwe akukhudzidwa ndi zachinyengo cha mtundu uliwonse muundunawu. +Za maufulu Nkhani ina yomwe idakhoma misomali yowawa pamitu pa Amalawi ndi ya maufulu omwe akatswiri akuti sadalemekezedwe monga momwe zimayenera kukhalira. +Malingana ndi mmodzi mwa akuluakulu oyanganira za maufulu, Billy Mayaya, maufulu ambiri adaphwanyidwa, monga ufulu wa maalubino omwe akuti amaphedwa ndi kuchitidwa nkhanza za dzaoneni. +Iye adatinso ufulu wina ndi wolandira nthandizo la mankhwala akadwala komanso chakudya. +Mayaya adatinso mchakachi, boma lidaonetsa kusalabadira maganizo ndi zofuna za anthu makamaka pa mmene lidagulitsira banki ya boma ya Malawi Savings anthu ndi magulu osiyanasiyana atayesetsa kuletsa. +Mkuluyu adatinso ufulu wa atolankhani udaponderedzedwa kwambiri mchakachi ngakhale kuti boma lidalonjeza kuti lidzapititsa patsogolo ufulu wa atolankhani kuti azidzatha kufufuza ndi kuulutsa nkhani popanda kusokonezedwa. +Mwachitsanzo, wayilesi ya Zodiak idaletsedwa kulowa kunyumba ya boma kuli zochitika pomwe wailesi ndi nyuzipepala zina zidaloledwa, kumeneku nkuwaphwanyira ufulu wotola ndi kuulutsa nkhani, adatero Mayaya. +Nduna yofalitsa nkhani za boma, Jappie Mhango, adati mpofunika kumpatsa nthawi yoti alingalire zonsezi asadayankhepo kalikonse kuti poyankha atsekeretu maenje onse. +Magetsi ndi madzi Mawu oti madzi ndi moyo adasanduka nthano mchaka chimenechi polingalira mavuto omwe adalipo kuti mpaka anthu kufika pomamwa madzi a mzitsime ndi zithaphwi chifukwa mipopi imakhala youma nthawi zambiri. +Malinga ndi akuluakulu a makampani opopa ndi kugawa madzi osiyanasiyana, vutoli lidakula kaamba ka vuto la magetsi omwenso adamvetsa kuwawa Amalawi. +Madzi timachita kupopa ndi mphamvu ya magetsi ndiye ngati magetsi kulibe, simungayembekezere kuti tipopa madzi okwanira nchifukwa mumaona kuti madzi pena atuluka pena asiya, adatero mmodzi mwa akuluakulu a makampaniwa, Alfonso Chikuni, wa Lilongwe Water Board. +Mkulu wa bungwe loyanganira za anthu ogula ndi kugwiritsa ntchito zinthu zosiyanasiyana, John Kapito, adati kulanda anthu madzi ndi magetsi ndi chilango chowawa kwambiri potengera ndalama zomwe anthuwa amapereka kumakampaniwa. +Chodabwitsa nchakuti mabilu a madzi ndi magetsi mmene alili kukwera chonsecho nthawi zambiri kumakhala kulibe. Anthu amangokhalira mumdima ndi kumwa madzi osalongosoka, adatero Kapito. +Anthu ambiri makamaka a mabizinesi adandandaula kuti kuthimathima kwa magetsiwa kudasokoneza bizinesi moti ena adataya katundu wambirimbiri yemwe adaonongeka panyengo yomwe kudalibe magetsi. +Za makhalidwe Kapito adati moyo mchakachi udawawa zedi potengera momwe mitengo ya zinthu imakwerera pomwe mapezedwe a ndalama adali ovuta kwambiri. +Iye adati kusakolola bwino kwa chaka chatha, kuvuta kwa malonda a fodya ndi mabala a Cashgate ndi zina mwa zomwe zidachititsa kuti mmatumba mwa anthu muume, koma izi sizidamange buleki ya kakwenzedwe ka mitengo ya katundu. +Kunena zoona Amalawi adamva ululu mchaka chimenechi. Ndalama zimasowa koma si momwe zinthu zimakwerera mtengo. Kayendetsedwe ka chuma nako kadali kodwalitsa mutu; zimangokhala ngati palibe woyendetsa, adatero Kapito. +Iye adati chodandaulitsa kwambiri nchakuti mayankho omwe ankaperekedwa pamavuto onsewa sadali ogwira mtima, mmalo mwake zimakhala ngati kunyogodola anthu omva kale kuwawa. +Chiyembekezo mu 2016 Akuluakuluwa adati Amalawi akufunika zakupsa mchaka chomwe tayambachi cha 2016 monga kusintha momwe zinthu zimayendetsedwera chaka chatha komanso kupatula ndale ndi kayendetsedwe ka boma. +Kapito adati ali ndi chiyembekezo kuti chaka chino, boma lichita chotheka kuchita kafukufuku wokwanira ndi kuweruza milandu ya Cashgate kuti maiko omwe adanyanyala kuthandiza dziko lino abwererenso. +Mayaya naye adati boma likhwimitse ndondomeko zotetezera maufulu a anthu, makamaka maalubino, ana ndi amayi omwe nthawi zambiri amakhala kunsonga ya nkhanza zosiyanasiyana. +Mkazi wansanje achekacheka mnzake Bwalo la milandu la majisitireti ku Mchinji masiku apitawa lidalamula kuti mayi wansanje amene adachekacheka mayi mnzake ndi mpeni pakhosi ndi kunkhope akagwire jere la miyezi 12 koma lidamumasula ponena kuti asadzapezekenso ndi mlandu wina kwa chaka chimodzi ndi theka. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Woimira boma pamilandu, Thom Waya, adauza bwalolo kuti mkazi wansanjeyo, Chimwemwe Fanizo, wa zaka 21, adafuna kuvulaza mwana wa mkazi mnzake wa miyezi 7 ndi mpeni ati popeza mwamuna wake ankapereka thandizo kwa mwanayo. +Wasiya kuonetsa mabala ake mchipatala Waya adati mpeniwo udasempha mwanayo yemwe adali kumsana ndi kulunjika pakhosi la mayi ake. Mbereko yomwe adaberekera mwanayo idamasuka moti adagwa pansi ndipo achisoni adamutola ndi kuthawa naye. +Izi sizidakondweretse Fanizo, yemwe adalikumba liwiro kuthamangitsa munthu amene adathawitsa mwanayo, mpeni uli mmanja. Komatu apa nkuti mkaziyo atamuchekacheka mnzakeyo malo anayi. Anthu adamugwira ndipo adapita naye kupolisi pamodzi ndi wovulazidwayo. +Izi zidachitika mmawa wa pa 6 January pa Mkanda Trading Centre. +Apolisi adamutsekulira mlandu wovulaza munthu, womwe womangidwayo adauvomera pamaso pa woweruza, majisitireti Rodwell Meja. +Malinga ndi Waya, bwalolo silidachedwe kugamula mlanduwo chifukwa woimbidwa mlandu sadatayitse khotilo nthawi povomera kulakwa. +Podandaulira bwalolo kuti limuganizire popereka chilango, Fanizo adati adapalamula mlanduwo chifukwa adachita kuputidwa ndi wodandaulayo, Tsala Wasiya, pokhala pachibwenzi ndi mwamuna wake. +Pogamula mlanduwo, Meja adati bwalo lake lidamupeza ndi mlandu wovulaza ndipo ayenera kulangidwa molingana ndi malamulo a dziko lino, koma adapereka chilango chosakhwimacho poganizira kuti adachita kuputidwa komanso poti sadatayitse bwalolo nthawi povomereza kulakwa kwake. +Meja adapereka chilango choti Fanizo akaseweze chaka chimodzi kundende koma adati kundendeko sapitako bola asapezekenso ndi mlandu kwa miyezi 18. Adamulola kuti azipita kwawo, mlandu watha. Adatinso ngati sakukhutira chi chigamulocho ali ndi ufulu kuchita apilo. +Msangulutso udacheza ndi Wasiya, yemwe ali ndi zaka 20, kuti umve mbali yake ndi mmene zidakhalira kuti zifike mpakana kuvulazidwa chonchi. +Iye adati adalidi paubwenzi ndi Daniel Nkhomo ndipo ubwenziwu utafumbira adapezeka ndi pakati. +Iye adati ngakhale awiriwa sadalowane, Nkhomo adali kupereka chisamaliro chonse chomwe munthu oyembekezera amafuna mpaka mwana adabadwa. +Koma ndidadabwa kuti pomwe mwana wanga adakwanitsa sabata zitatu, abambowa adakatenga mkazi wina kwa Msundwe ndipo adasiya kupereka chithandizo, iye adatero. +Wasiya adati koma patadutsa miyezi iwiri bamboyu adayambiranso kuthandiza mwana wakeyu ndipo awiriwa amatchayirana lamya mwanayu akadwala zomwe sizimamkomera mkazi mnzakeyo. +Tsiku lina ndidatumiza uthenga palamya kuti andiimbire kaamba koti mwana adali atadwala matenda otsekula mmimba. Mkazi wakeyu ndiye adandiimbira ndi kunditukwana, Wasiya adatero. +Iye adati mphuno salota sadadziwe kuti Fanizo adali ndi mangawa ndipo adakagula mpeni ndi kukanoletsa kumatchini ndi cholinga chofuna kuthana naye. +Wasiya adati patsikuli adali akuchokera kumsika ndipo Fanizo adamutchingira kutsogolo. +Adandifunsa kuti bwanji ndimaimba lamya ya mwamuna wake? Bwanji adandisiya ine nkutenga iyeyo ngati ndili naye mwana wake? Nkudzati ndipanga za iwe, pompo mpeni sololu kuti abaye mwana kumsana. Mpeniwu udafikira pakhosi panga, adalongosola Wasiya Iye adati koma adali wodabwa kuti ngakhale adavulazidwa chomwechi Fanizo ndi mfulu ndipo adampititsa kwawo. +Msangulutso udachezanso ndi Wasiya Titus, bambo wa mayi wovulazidwayu. +Iye adati sakudziwa kuti mlanduwu uli pati kaamba koti atafufuza kupolisi ya Mchinji adauzidwa kuti Fanizo adamasulidwa ndi abwalo la milandu. +Abwalo la milandu sadamve mbali ya mwana wanga yemwe sakupezabe bwino, kodi adamtulutsa bwanji ife okhudzidwa kulibe? Komabe ndipita konko kuti ndikamve umo zidayendera, adatero Titus. +Pakalipano Wasiya wanenetsa kuti zivute motani akufuna mwamunayu amukwatire basi. +Ine ndikufuna mwamunayu andikwatire chifukwa wandipatsitsa mabala, moti amuna ena sadzandisiriranso ayi. Ndipo mkazi wakeyu achita bwanji nsanje ndi ine, popeza ine ndiye ndidali woyamba ndipo ndimafunika kuchita nsanjezo ndineyo osati iyeyo wachiwiri ayi, adalankhula motsindika Wasiya. +Pomwe Msangulutso udacheza ndi mwamunayo Lachinayi lapitali palamya, iye adati Wasiya adali mkazi wachibwenzi pomwe Fanizo adali wapanyumba. +Apolisi akwidzinga anthu 10 ku Neno Akuwaganizira kuti adatengapo mbali kupha agogo anayi Apolisi mboma la Neno Lachinayi adanjata anthu 10 powaganizira kuti adatengapo mbali pa imfa za agogo anayi omwe adachita kuphedwa ndi anthu olusa powaganizira kuti ndiwo adalenga mphenzi yomwe idapha mtsikana wa zaka 17, Flora Kanjete, Lolemba lapitalo. +Mneneri wa apolisi mbomalo, Raphael Kaliati, polankhula ndi Msangulutso Lachitatu lapitali, adati kufikira Lachitatulo apolisi adali asadamange wina aliyense wokhudzidwa ndi kuphwedwa kwa anthu okalambawo podikira kuti bata likhazikike kaye kuderalo kuti ayambe bwino kufufuza za imfazo. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Koma mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, adalowererapo polamula mkulu wa apolisi Lexten Kachama kuti nkhaniyi aifufuze mmangummangu kuti chilungamo chioneke malinga ndi malamulo a dziko lino ndipo kuti ngati ena apezeka olakwa pamlandu wakupha alandire chilango choyenera. +Malinga ndi chikalata chochokera kunyumba ya boma chomwe adachitulutsa Lachitatu, mtsogoleri wa dziko linoyu adati adali wachisoni komanso wokhumudwa kwambiri ndi imfa za agogowo kaamba kowaganizira za ufiti. +Chikalatacho chidati: Pulezidenti [Mutharika] akuti anthu okalamba ayenera kulandira ulemu komanso chitetezo nthawi zonse ndipo boma lake silidzalola kuti okalamba azitonzedwa kapena kuvutitsidwa mnjira ina iliyonse mdziko muno. +Ndipo pofika Lachinayi, malingana ndi mneneri wa polisi pa Neno, anthu 10, kuphatikizapo anyamata asanu a zaka za pakati pa 13 ndi 18, adanjatidwa ndipo ali mmanja mwa apolisi powaganizira kuti ndiwo adakonza upo wopha agogowo. +Ena mwa omangidwawa ndi Staford Chifundo, wa zaka 36; Amosi Sida, wa zaka 32; Samuel Kaudzu, wa zaka 20; John Harry, wa zaka 21; ndi Lex Mayenda, wa zaka 19. Onsewa, kuphatikizapo anyamata achisodzerawo, akuti mpachibale ndi agogo adaphedwawo. +Kaliati adati anthu khumiwa awatengera kubwalo la milandu la majisitireti ku Neno komwe akaipereke mmanja mwa bwalo lalikulu la High Court poti ndilo lili ndi mphamvu zozenga milandu ikuluikulu monga ya kupha. +Iye adati zofufuza zidakali mkati ndipo pali chiyembekezo choti lamulo ligwirapo ntchito pa onse okhudzidwa ndi nkhani yoziziritsa nkhongonoyi. +Nalo bungwe la Malawi Law Society lidati ndi lokhumudwa ndi imfa za agogowo, omwe adaphedwa pazifukwa zopanda mchere, pongowaganizira za ufiti kaamba ka ukalamba wawo. +Omwe adakonza chiwembu chopha agogowa ayenera afufuzidwe bwinobwino ndipo akapezeka ayenera akayankhe mlandu kubwalo la milandu ndi kulandira chilango choyenera akapezeka olakwa. +Bungwe lathu ndi lokonzeka kupereka maloya kuti athandize boma pozenga milanduyo, chatero chikalata chomwe a bungweli atulutsa pambuyo pa kumva za nkhani yomvetsa chisoniyi, chomwe chidasainidwa ndi pulezidenti wa bungweli John Suzi-Banda ndi mlembi Khumbo Bonzoe Soko. +Oganiziridwawo adamenya agogowo mpaka kumpha zitangodziwika kuti mphenzi yapha mtsikanayo dzuwa likuswa mtengo. Malinga ndi Kaliati, anthuwo akukhulupirira kuti mphenziyo idali yokonzedwa ndi agogowo, omwe adali pachibale. +Mboma la Neno muli vuto la mvula. Chiyambireni chaka chino, mvula yagwa masiku 8 okha koma mphenzi zakhala zikunganima ndi kupha anthu kumeneko. +Agogowo ndi Eliza Enosi Kanjete, wa zaka 86; Elenefa Kanjete, wa zaka 76; Byson Kanjete, wa zaka 73; ndi Idesi Julias Kanjete, wa zaka 69. Onsewa adali a mmudzi mwa Chimbalanga 1. +Agogowo adaikidwa mmanda Lachiwiri limodzi ndi mtsikanayo adaphedwa ndi mphenzi uja. +Chilango cha kunyonga chiutsa mapiri pachigwa Ndawala yofuna kubwezeretsa chilango choti wopha mnzake naye aphedwe yavumbulutsa maganizo osiyanasiyana pakati pa mafumu, anthu ndi boma. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndawalayi idachitika Lachinayi lapitali mumzinda wa Lilongwe pomwe phungu wa kummwera kwa boma la Mulanje Bon Kalindo adatsogolera khamu la anthu kukapereka chikalata ku Nyumba ya Malamulo chopempha kuti chilangochi chibwerere. +Kumayambiriro a sabata yathayi, ndawalayi isadachitike, nduna ya zofalitsa nkhani Patricia Kaliati idanenetsa kuti boma lilibe maganizo obwezeretsa chilangochi potengera pangano la maiko onse. +Kaumba akaseweza moyo wake wonse kundende Dziko la Malawi lidasayina nawo mapangano ambirimbiri okhudza za ufulu wa anthu ndiye sitingabwerere mmbuyo nkuyamba kuphwanya pangano lomwe tidasayina tokha, adatero Kaliati polankhula ndi atolankhani ku Nyumba ya Malamulo. +Koma mafumu ena akuluakulu monga Chindi wa ku Mzimba mchigawo cha kumpoto ndi Kabudula wa chigawo cha pakati adati iwo akuona kuti munthu wopha mnzake akuyenera nayenso aphedwe, osanyengerera. +Chindi adati koma mpofunika kulingalira mofatsa pogamula milandu yotereyi kuti chilungamo chioneke kuti kodi adapha mwangozi kapena dala kuti zilangozo ziperekedwe. +Kupha kuli pawiri-mwadala ndi mwangozi. Apapa tikhazikike pa wopha mwadala monga momwe opha maalubino amachitira. Amenewa akuyenera kuphedwa basi, osawanyengerera, ayi, chifukwa nawonso sadanyengerere mnzawoyo, adatero Chindi. +Naye Kabudula adati palibe njira ina yoposa kupha anthu otere chifukwa moyo wawo uli ngati zilombo zolusa zomwe zingaononge mtundu. +Onsewa adasemphana ndi mfumu Chapananga ya ku Chikwawa mchigawo cha kummwera yomwe idati chilango chakupha si chilango chabwino, bola ndende moyo onse. +Kwa ine zakuphazo ayi, bola atati opha mnzake azikakhala kundende moyo wake wonse basi, adatero Chapananga. +Anthu osiyanasiyana omwe adacheza ndi Msangulutso adaperekaso maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya chilangochi. +Bernadette Kaonga, wa ku Area 49 mumzinda wa Lilongwe, adati iye sangavomereze kuti anthu aziphedwa. Iye adati njira yabwino nkupeza njira yoti zophanazo zitheretu kapena, apo ayi, kundende moyo wonse. +Mnzake yemwe adali naye limodzi panthawiyo, Mary Molosi, adati iye akuganiza kuti njira yomwe ingathetse zophanazo ndi chilango chophedwa, basi. +Chigodola chavuta ku Nsanje Ngombe 70 mboma la Nsanje zikutsalima, pamene 65 000 kumeneko zili pachiopsezo chotenga matenda a chigodola amene abonga mbomalo. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kafukufuku wa unduna wa zamalimidwe wa pa 8 January udapeza kuti matendawa abukanso mbomali patangodutsa mwezi matendawa atazizira mboma la Chikwawa. +Kutemera ngombe kudagundika ku Chikwawa Malinga ndi mkulu wa Shire Valley Agriculture Development Division (ADD), Jerome Nkhoma, panopa ndiye matendawa afika pagwiritse chifukwa sabata yathayi nkuti ngombe 60 zitagwidwa koma pofika sabata ino ngombe zodwala zidafika pa 70. +Nkhoma adati ziweto za kudipi ya Bangula ku Magoti Extension Planning Area (EPA) mbomalo ndi zomwe zili pampeni wotenga matendawa. +Padakalipano boma lalengeza kuti kuyambira tsopano, kupha nyama ya mbuzi, ngombe, nkhumba komanso nkhosa nkoletsedwa mbomalo. +Kalata yomwe boma kudzera muunduna wa zamalimidwe idatulutsa ndipo idasayinidwa ndi mlembi mu undunawu Erica Maganga, idaletsa kugulitsa komanso kulowetsa kapena kutulutsa ziwetozi mbomalo pokhapokha matendawa atakatuka. +Chibukireni matendawa mboma la Chikwawa, ngombe 91 965 ndizo zidalandira katemera mchigawo choyamba cha katemerayo. +Chikwawa ndilo lidali boma loyamba kubuka matendawa kutsatira kusefukira kwa madzi komwe kudachitika pa 12 January 2015. +Koma undunawu wati ntchito yolandiritsa katemera ku ziweto zomwe zakhudzidwa ndi matendawa kuli mkati. +Mnyamata asiya sukulu chifukwa cha mantha A makhumbira atakhala msirikali, koma popanda moyo ntchitoyi singatheke. Lero Christopher Robert, mnyamata wachialubino, wasankha kaye moyo posiya sukulu yomwe ati ikadamuphetsa. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Zochitika pa 6 May 2016, pamene mnyamata wina wosamudziwa adafika pasukulu pawo kudzamutenga ndi zomwe zachititsa kuti thupi la Christopher lichite tsembwe ndi mantha kuti moyo wake ukhoza kukhala pachiswe ndipo walembera aphunzitsi ake kuti wasiya sukulu. +Mphunzitsi wamkulu pasukulu ya Mwatonga, kwa T/A Kasumbu mboma la Dedza, wauza Msangulutso kuti patsikulo mnyamata wina adafika pasukulupo nkunena kuti watumidwa kudzamutenga Christopher, wa zaka 18, yemwe ali kalasi 6, chifukwa akumufuna kupolisi ya Dedza. +Amati watumidwa, koma nditaimba kupolisi, adandiuza kuti ndimumange, ndipo ndidaterodi, adatero mphunzitsiyu, Felix Mussa. +Akuti moyo wake uli pachiopsezo: Christopher Adatsagana ndi mayi ake a Christopher ndi achitetezo cha mmudzi ulendo kupolisi komwe ati adakadzidzimuka akuuzidwa kuti amupepese mnyamatayo chifukwa chomunjata popanda chifukwa. +Ine limodzi ndi mayi a Christopher komanso achitetezo tidamupepesa ndipo adamumasula pomwepo, adatero Mussa. +Mnyamatayo, yemwe ndi wabisinesi, adauza Msangulutso kuti: Adati ndikatenge amfumu, makolo a mwana ndi mwanayo kuti abwere kupolisi adzafunse zina ndi zina chifukwa amati kunyumba kwawo kudapitako anthu amene ankafuna akamube, adatero iye. +Mathedwe a nkhaniyi adatutumutsa Christopher ndipo mantha adayanga thupi lake nchifukwa adaganiza zolembera mphunzitsi wamkuluyu kuti sukulu waisiya. +Zikomo Ahedi. Muli kudziwitsidwa kuti ndayamba ndasiya sukulu chifukwa cha nkhani yomwe inachitika Lachisanu. Ndiye ndaona kuti sindingathe kuphunzira chifukwa ndingathe kumakhala ndi maganizo komanso poweruka ndimakhala ndekha ndiye njira ndiyaitali chosadziwika chondichitikra munjiramu pamene ndili ndekha paja poyamba ndinafotokoza kale ndiye panopa ndili pankhawa ngati pangakhale kusamvetsa pazomwe ndanenazi munene tsiku kuti ndibwere kuti tidzakhambirane. Zimene ndinafuna kudziwitsani ndi zomwezi. Ndine Christopher, ikutero kalaya yomwe adalemba Christopher. +Mtolankhani wa Msangulutso atamupeza kunyumbako, kudali kovuta kuti alankhulane naye. +Adadzitsekera mnyumba, ngakhale ahedi a Mussa, amfumu komanso achibale ena adamuuza kuti asaope, iye adakanitsitsa poganiza kuti mtolankhaniyu wabwera kudzamuba. +Padatha mphindi 30, ndipo Christopher adatuluka, mayi ake atakambira naye. Nkhope yakugwa, iye adakhala patali ndi mtolankhaniyu. +Ndili wachisoni kuti ndasiya sukulu. Ndimakhumbira nditakhala msirikali, koma basi sindidzakhalanso msirikali chifukwa sukulu ndasiya, adayamba kufotokoza Christopher, amene adakhala nambala 4 mkalasi teremu yatha. +Iye adati sakuganizanso atabwerera kusukulu chifukwa chilungamo sichidayende pankhani yake. +Ndi bwino andiphere pakhomo pano kusiyana kuti akandiphere kusukulu. Izi zidandipatsa mantha ndipo ndidaganiza zolemba kalatayo kuti ndasiya sukulu. Nakonso kukwaya sindikupita ndipo ndikungodzitsekera mnyumbamu, adatero Christopher, amene bambo ake banja lidatha ndi mayi ake. +Wachiwiri kwa mneneri wa polisi ya Dedza, Cassim Manda, adavomera kuti mnyamata amene adapita kusukulu ya Christopher adamutulutsa chifukwa adamangidwa mlandu wosaudziwa. +Tikufuna tifufuze kaye ndiye tamutulutsa. Kungoti pali zomwe zidachitika ndiye tikufufuza, adatero Manda, ponena kuti sangayankhe mafunso ambiri pafoni koma pamaso. +Ngakhale mutu weniweni wa nkhaniyi sukudziwika bwinobwino, Christopher akuti sabwereranso kusukulu, komwe amayenda makilomita 7 kuchoka kunyumba kwawo. +Padakalipano mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika wapempha amipingo kuti athandizepo kuti mchitidwe wopha ndi kusowetsa achialubino otheretu. +APM akuzemba PAC Akatswiri a ndale Othirira ndemanga pa ndale mdziko muno ati zimene mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika wachita posakumana ndi a bungwe la Public Affairs Committee (PAC) kuti amve zomwe msonkhano wawo udagwirizana pa za mmene zinthu zilili mdziko muno zikuonetsa kuti mtsogoleriyu akuzengereza dala kuti nkhaniyi izizire ndi kuiwalika. +Aphunzitsi awiri a kusukulu ya ukachenjende ya Chancellor College omwenso ndi anamatetule pa nkhani za ndale, Boniface Dulani ndi Joseph Chunga anena izi msabatayi pothirapo ndemanga pa kulephereka kwa mkhumano wa akuluakulu a bungweli ndi mtsogoleriyu. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Akuti mpata sakuupeza: Mutharika Kawiri konse Mutharika wasintha nthawi yokumanirana ndi akuluakulu a PAC ponena kuti ndi wotanganidwa ndi ntchito zina. +Poyankha PAC imayembekezera kukumana ndi Mutharika pa 25 February koma zidakanika ndipo boma lidati mkhumanowu uchitika pa 29 March zomwenso zalephereka. +Mkulu wa bungweli la PAC Robert Phiri wati iwo adafika mumzinda wa Blantyre kuti akumane ndi Mutharika koma mwadzidzidzi adangomva kuti nkhumanoyo yalephereka. +Izi zachititsa kuti PAC ilephere kufotokozera Mutharika zomwe msonkhano wawo, womwe udachitika pa 17 February chaka chino, udagwirizana. +Koma akadaulowa akuganiza kuti Mutharika akungozemba chabe osati watanganidwa ndipo ati izi sizingachitire ubwino anthu amene akuyembekezera mayankho pa mfundo zomwe zikukhudza Amalawi. +Dulani adati zomwe akuchita Mutharika ndi kuzemba chabe ncholinga choti nkhani zomwe zidatuluka ku PAC zizizire ndi kuiwalika. +Akungozemba chabe. Inde, Pulezidenti amakhala wotangwanika, koma sindikukhulupirira kuti angalephere kupeza nthawi yokumana ndi a PAC. +Chomwe tingadziwe, dziko lino lili pamavuto aakulu kotero tikuyenera kupeza mayankho mwachangu ndipo izi ndi zomwe bungwe la PAC lidachita kumva maganizo kwa anthu osiyanasiyana, adatero Dulani. +Koma mneneri wa boma, Jappie Mhango, wati si zoona kuti Mutharika akuzemba, koma kuti mtsogoleriyu amakhala wotanganidwa ndi ntchito zambiri. +A Pulezidenti amayeneradi kukumana ndi a PAC koma sizidatheke chifukwa cha nkhumano zinazo zomwe akuyenera akakhalepo, koma si kuti akuthawa, ayi, adatero Mhango. +Mhango wati tsiku lomwe akumane ndi akuluakulu a PAC awadziwitsa akuluakuluwa koma izi zichitika Mutharika akakhala ndi mpata wotero. +Kadaulo wina pandale ku Chancellor College, Joseph Chunga, wati Mutharika ali ndi nthawi yambiri yomwe angakwanitse kukumana ndi PAC koma izi zikungoonetsa kuti sakufuna. +Ndikuganiza kuti mtsogoleriyu akungofuna kugula nthawi kuti akonze zomwe PAC idakambirana ncholinga choti pamene azikumana nawo akhale atakonza zinthu zina, adatero Chunga. +Chunga watinso Mutharika adauzidwa kale ndi akuluakulu a boma amene adali nawo pamsonkhanowo za zomwe adakambirana. +Si kuti sakudziwa zomwe zidakambidwa, zidali mmanyuzipepala komanso nduna zake zikuyenera kuti zidamufotokozera, komabe ngakhale izi zili chonchi, akuyenera kukumana ndi a PAC chifukwa ndi oima paokha, adaonjeza. +Msonkhano wa PAC mwa zina udagwirizana kuti Mutharika akonze zinthu pano. Izi ndi monga kusowa kwa chimanga. Zinanso zomwe adagwirizana nkuti boma lichotse zinthu zina zomwe likuchita pofuna kupeza mavoti monga kukweza mafumu ndi pologalamu yomangira anthu nyumba ya Cement and Malata Subsidy. +Mfumu yoba mopusitsa igamulidwa mawa Bwalo lamilandu la majisitileti ku Ntchisi mawa likuyembekezeka kupereka chigamulo kwa mfumu ina Lachisanu idaepezeka yolakwa pamlandu wakuti inkabera anthu powanamiza. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Malinga ndi mneneri wapolisi ya Ntchisi Gladson Mbumpha, wogamula Young Ngoma adapeza nakwawa Nyalapu (dzina lenileni Fraser Vesiyano) yolakwa pamlandu woti idapusitsa anthu ozingwa a mmudzi mwa Chiwere kuti iwathandiza kugula feteleza ku Admarc ya mmudzi mwake. +An artistic impression of a court room Ngoma adati mchitidwe wa nyakwawawo ngobwezeretsa chitukuko mmbuyo chifukwa nkuphwanya ufulu wa anthu ovutika. Chigamulo chiperekedwa Lolemba chifukwa samamva bwino mthupi, adatero Mbumpha Lachisanu. +Malinga ndi Mbumpha, Nyalapu, yemwe ndi wa zaka 33, adapusitsa anthu ozingwa a mmudzi mwa Chiwere kuti awathandiza kugula feteleza ku Admarc ya mmudzi mwake. +Iye adamata phula anthuwo kuti ali ndi njira zomwe angachite kuti athe kuwagulira fetelezayo koma pambuyo pake adayamba kuchita njomba. +Anthuwo adali ndi makuponi koma zikuoneka kuti mmudzi mwawo, Admarc yomwe amadalira kudalibe feteleza ndiye mfumuyo itamva idaona ngati mwayi okhupukira nkuuza anthuwo kuti iwathandiza, adatero Mbumpha. +Iye adati mfumuyi idauza anthuwo kuti asonkhanitse makuponi komanso asonkhe ndalama zomwe zidakwana K148 500 nkumupatsa ndipo adagwirizana kuti adzabwere tsiku lotsatilalo kudzatenga fetereza wawo. +Njomba zidayamba kuwoneka anthuwo atabwera chifukwa mfumuyo idawawuza kuti abwerenso tsiku linzakero ndipo masiku amapita akuwuzidwa zomwezomwezo. +Anthuwo atatopa adangoganiza zopita kwa mkulu wa pa Admarc yomwe imanenedwayo ndipo mkulu wa pamenepo Yasinta Jere adawauza kuti mfumuyo idagula feterezayo pa 11 January 2013, adatero Mbumpha. +Alubino akufuna chilungamo Bambo wachialubino ku Ntcheu wati akufuna chilungamo pankhani yake yomwe akuloza chala mkulu wina wabisinesi kuti adamutsekera mgolosale ndi kumubera ndalama zokwana K103 000, komanso kumuopseza kuti amupha. +Kudandaula kwake kukubwera pamene bwalo la Mozambique pa 16 February lidagamula kuti woganiziridwayu alibe mlandu kusiya mkuluyu, yemwe ndi mphunzitsi, ali kakasi, kusowa mtengo wogwira. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Apolisi mdziko la Mozambique ndi Malawi atsimikiza kuti nkhaniyi idazengedwadi mdziko la Mozambique. +Mkulu wachialubinoyu, Charles Chidambukira Ndau, yemwe akuphunzitsa pa Chilobwe LEA ku Lizulu mbomali, wauza Tamvani kuti pa 6 February adatsekeredwa mshopu ya wamalonda wina yemwe adamuopseza kuti amupha akakuwa. +Ndidapita kukagula malata ndipo ndili mshopumo, adauza mnzake wogwira naye ntchito kuti atseke zitseko. Kenaka adati ndamuchita chitaka ponena kuti K76 000 yake yasowa. +Adati nditulutse ndalama zanga zonse ndipo ndidatulutsa K103 000 yomwe ndidali nayo ndipo adandilanda K76 000 ndi kundibwezera K27 000, koma adandilandanso nkuingambangamba. +Ndimaganiza kuti anditulutsa, koma sadatero ndipo adayamba kundiopseza kuti andipha. Adandimanga nkukanditsekera kuchipinda cha shopuyi, yomwe ili mbali ya Mozambique mmalire ndi dziko la Malawi, adatero Ndau. +Iye adati polingalira kuti tsiku lakufa lafika, adapemphera ndipo mwamwayi zingwe adamumangira zija zidalera. Mwamwayinso adali ndi foni ndipo adaimbira mwana wake kumuuza kuti watsekeredwa mshopumo ndipo akufuna kumupha. +Adanditsekera cha mma 8 koloko mmawa ndipo anthu amatulukira cha mma 11 koloko. Adafuna kuphwanya shopu, kenana apolisi a Mozambique adatulukira kudzandipulumutsa komanso adamumanga yemwe adanditsekerayo ulendo kupolisi yawo, adatero Ndau, yemwe ali ndi ana 6. +Atachoka kupolisiko, Ndau akuti adapita kupolisi ya Lizulu kumbali ya Malawi kukalembetsa sitetimenti ya momwe nkhaniyi idakhalira. +Amaganiza kuti nkhaniyi ikambidwa mdziko la Malawi potengera kuti wodandaula ndi woganiziridwa onse ndi nzika za ku Malawi, sizidatero. Bwalo la Villa Ulongwe mdziko la Mozambique ndilo lidazenga mlanduwo ndipo akuti lidagamula kuti palibe mlandu. +Pa 15 February ndidalandira uthenga kuti ndipite kukhoti la ku Villa Ulongwe ndipo nditapitako pa 16 February adandiuza kuti chigamulo cha nkhani yanga chidali choti palibe mlandu. Adati nkhani idazengedwa pa 12 February pamene ine sindimadziwapo kalikonse kuti yakambidwa, adatero mkuluyu. +Ndau adati ngakhale adakagwada kupolisi ya Lizulu, padalibe thandizo ndipo mmalo mwake wapolisi wa ku Mozambique ndiye adachita chotheka kuti ndalama zake amubwezere. +Yemwe adanditsekerayo atabweza ndalamazo, adadziwitsa apolisi ya Malawi kuti asasainirane ndipo ndalama zonse K103 000 adandibwezera. Pamenepa ndipo pakundidabwitsa ine, ngati palibe mlandu, bwanji adabweza ndalamazo? akudabwa Ndau. +Mkulu wa polisi ya Lizulu mdziko la Mozambique, Philip Jackson, watsimikiza kuti nkhaniyi idakazengedwadi ku Villa Ulongwe chifukwa idachitikiranso mdzikomo. +Tikagwira anthu amene aba ku Malawi, timawapatsira apolisi anzathu a ku Malawi, nawonso Amalawi akagwira anthu amene apalamula mlandu mdziko lathu amatipatsira. +Nkhani mukunenayo idachitikira kuno ku Mozambique chifukwa shopuyo ili mdziko lathu ngakhale onsewo ndi Amalawi. Nchifukwa tidaitengera kukhoti la ku Villa Ulongwe, adatero Jackson. +Jackson adati mlandu womwe udapita kubwaloko ndi wotsekera munthu mnyumba, osati wofuna kumupha, monga mwini wake akunenera. +Nkhani zofuna kupha anthu achialubino nzovuta ngakhale mdziko lathu, ndiye tidamutsegulira mlandu wotsekera munthu mnyumba, adatero. +Wapolisi wina papolisi ya Lizulu mbali ya ku Malawi, yemwe adati tisamutchule dzina, naye adatsimikiza kuti nkhaniyi idazengedwadi mdziko la Mozambique koma adati ngati tifuna kudziwa zambiri tiyankhule ndi a kulikulu la polisi. +Wapolisiyu adatsimikizanso kuti Ndau adakadandaula kupolisi yawo koma chomwe adangomva nkuti chigamulo chaperekedwa kale ku Mozambique. +Koma wachiwiri kwa mneneri kulikulu la polisi mdziko muno, Thomeck Nyaude, wati chomwe akudziwa nkuti nkhaniyi ili mmanja mwa khoti la Malawi. +Nkhaniyo ndikuidziwa, chomwe ndinganene nkuti nkhaniyi ikalowa mkhoti tsiku lina lililonse. Zoti kwaperekedwa chigamulo ku Mozambique, ine sindikudziwa. Ngati anthuwo ndi Amalawi, zitheka bwanji kuti mlandu wawo ukazengedwe ku Mozambique? adatero Nyaude, koma sadatchule khoti lomwe lizenge nkhaniyi. +Mkulu wa bungwe la Association of Persons with Albinism, Boniface Massah, wati nkhaniyi akuidziwa ndipo nawonso ndi odabwa ndi chigamulo komanso chifukwa chomwe idakazengedwa mdziko la Mozambique. +Tikufuna kumvetsa ngati kuli kovomerezedwa kuti nkhaniyi ikazengedwe mdziko lina, koma nkhani yathu yaikulu ndi zotsatira za chigamulo kuti adapeza kuti palibe mlandu, adatero Massah. +Iye adati akudikirabe yankho pa kalata yomwe adalembera unduna woona za anthu olumala yomwe adapempha kuti chigamulochi chiunikidwe asanakamangale kubwalo lina. +Katundu wobwera ku Malawi ali pachiopsezo ku Mozambique Magulu a zachifwamba mdziko la Mozambique akuchitira mtopola galimoto zonyamula katundu wosiyanasiyana wobwera mdziko muno kuchokera kumaiko ena podutsa mdzikolo. +Pali malipoti oti mdzikomo muli nkhondo yapachiweniweni pakati pa asirikali a boma ndi zigawenga za chipani chotsutsa cha Renamo chomwe mtsogoleri wake ndi Afonso Dhlakama, koma boma la Mozambique lakhala likutsutsa malipotiwo ngakhale anthu ena zikwizikwi athawa mdzikomo kudzapeza mpumulo mdziko lino. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mtopolawu udayamba Lachitatu sabata yatha pomwe maguluwo adatentha galimoto ina yomwe idanyamula mafuta a petulo wandalama zokwana pafupifupi K28 378 800 yemwe amabwera mdziko muno. +Mtopolawu usadaiwalike, maguluwo adatenthanso galimoto zina zitatu Lachisanu masana ndipo ziwiri mwa galimotozo zidanyamulanso mafuta ndipo msabata imodzi yokha, galimoto zoyatsidwa zakwana zisanu. +Chiwembuchi chikuchitika kwambiri kwa galimoto zodutsa njira ya Tete ndi Beira ndipo maguluwo sakusankha kochokera kapena kopita galimotozo. +Malingana ndi mkulu wa bungwe la makampani oitanitsa mafuta mdziko muno, Enwell Kadango, ndalama zokwana pafupifupi K70 miliyoni zapita mmadzi kaamba ka ziwembuzi ndipo iye adati iyi ndi nkhani yoipa pamalonda. +Mwachidule, galimoto iliyonse yonyamula mafuta, imanyamula mafuta a ndalama zapakati pa K22 miliyoni ndi K23 miliyoni ndiye mukawerengera ndalama zomwe zamwazika nzambiri zedi, adatero Kadango polankhula ndi Tamvani. +Potsatira zokambirana pakati pa maiko a Malawi ndi Mozambique, dziko la Mozambique lidatumiza asirikali ake kuti azikaperekeza galimoto zotuluka ndi kulowa mdziko muno podzera mdzikolo. +Mneneri wa unduna woona za maubale a dziko lino ndi maiko ena, Rejoice Shumba, adatsimikiza nkhaniyi. +Obzala nthawi ya maliro athothedwa Thambo likagwa mmudzi, aliyense amayenera ayandikire chifupi ndi siwa kuti athandizane nthawi ya zolemetsayi. Kudagwa zovuta mmudzi mwa Mazale kwa Senior Chief Kapeni mboma la Blantyre. Nthawi yokagoneka mfumu itakwana, ena ndiye adali kalikiriki kubzala. Izi zidakwiyitsa adzukulu. Ndiyetu kudali kuwathamangitsa. BOBBY KABANGO adali nawo komweko ndipo adacheza ndi mfumu Mazale pa za anthu ophwanya mwambowa motere: Ulendo wa kumanada: Aliyense akuyenera kupezekako Pepanitu mfumu Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Aaa lekani wawa. +Choyamba tatifotokozereni za zovutazi Mmudzi muno tidali ndi kamnyamata kena kamene kadali msangulutso wa aliyense, kochezeka komanso kakhalidwe labwino. Kanangodwala katapita ku Bangwe kwa makolo ake. Kukatengera kuchipatala basi ndagona pano. Mnyamata ameneyu adali Manuel German. +Pepani ndithu, paulendo paja tidaona anthu akuthamangitsana, chidachitika nchiyani? Sindidziwa kuti ndinu amtundu wanji, koma kwathu kuno, maliro akachitika, timayenera tonse tilire limodzi. Zilibe kanthu kuti watangwanika komabe timayenera tisonkhane chifukwa izi ndi zadzidzidzi, palibe amene amafuna kuti zitero. Ndiye chidachitika apa nchakuti pamene timati tinyamuke kuperekeza mfumu yathu, basitu tidangodabwa kuona anthu ena akubzala mbewu zawo mminda. +Ndiye adzukulu adawalondola kuti amve vuto lawo lidali chiyani. +Adangowalondola? Ndaonatu akuwathamangitsa Eya ndiye kuwalondolako. Kudali kumva za vuto lawo kuti azibzala pamene tonse tikulira. Adawalonda mpaka adataya mbewu koma cholinga kudali kuwatenga. Mwamvanso adzukulu akudandaula kumanda kuja, zimenezo ndi zolakwika kumagwira ntchito pamene anzako akulira. +Kodi nkulakwa kugwira ntchito pamene ena ali pachisoni? Kwambiri, masiku ano mwambo wathu sukutsatidwanso. Umenewu ndi mlandu ndithu ndipo siziyenera zizitero. Ngati mmudzi wina mwachitika zovuta, timayenera midzi yonse yoyandikana tilire pamodzi. +Kodi Chipuwa wabwerera kumalonda? Luso la Richard Chipuwa, goloboyi wa Flames komanso Mighty Be Forward Wanderers ndi losayamba. Pa 15 January chaka chino adachoka mdziko muno ulendo ku Mozambique koma sadapatsidweko mwayi wosewera mpaka wabwerera kumudzi sabata yathayi. Kodi zatani? Msika wasowa? BOBBY KABANGO adacheza naye kuti amve zambiri motere: Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Manja antchito: Chipuwa akuti ayese nawo ku Wanderers Kodi mwabwera, mfumu? Tafikatu amwene, tasowanatu koma mfumu. +Mwalemeratu, mpaka mwabwera ndi galimoto? Hahaha nanunsotu musayambe apa Mwafika liti, mfumu? Sabata yathayi, koma ndilipo chifukwa ndikufuna ndisewere mdziko momwemuno kwa chaka chino ndipo ndibwerera chaka chamawa. +Ku Mozambique kwataninso? Mwathawa nkhondo kapena? Ma documents ondiloleza kusewera mpira kumeneko sakuoneka mu system. Federation ya ku Maputo idandiuza kuti ma documents sakuoneka ngakhale Wanderers idatumiza. Izi zapangitsa kuti Chingale FC isandigwiritse ntchito. Chichokereni muja palibe chatheka ndiye ndaganiza kuti ndibwerere kumudzi kaye. +Vuto nchiyani kuti asaoneke? Nanenso sindikumvetsa, koma Wanderers idanditsimikizira kuti yatumiza. +Osati wathawa nkhondo? Hahaha! Mayazi, amwene, sizikukhudzananso. +Ukutanthauza kuti sumasewera chichokereni kuno? Ayi ndithu, ngati ndimasewera ndi magemu opimana mphamvu komanso ku training. +Apa simwatheratu, mfumu? Mumaka koma? Ndine wampira, ndimadziwa ntchito yanga ndipo kupatsidwa mpata muonanso, mfumu. +Panopa ndiye ulowera timu iti? Ndikufuna ndikambirane ndi Wanderers, zikatheka mwina ndisewera kumeneko. Zikakanika ndiye ndisewerera timu iliyonse yomwe timvane. +Komatu pochoka zimamveka ngati mwakangana ndi a Wanderers Ayi, padangokhala kusamvetsetsana koma zonse tidakambirana. +Boma lilonga mafumu 250 Boma kudzera muunduna wa za maboma aangono latsimikiza kuti mafumu 250 aikidwa pamndandanda wolandira nawo mswahara kupangitsa kuti ndalama zopita ku thumba la mafumuwa zikwere. +Nduna ya maboma aangono, Kondwani Nankhumwa, wati nkhani ya mafumu ili choncho chifukwa ntchitoyi idayambika kale ndi mtsogoleri wakale Joyce Banda ndipo boma la DPP likungopitiriza ndondomekoyi. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mafumuwa adawakweza ndi mtsogoleri wakale Joyce Banda koma adali asadawaike pamndandanda wolandira ndalama komanso ena adali asadalamulidwe kuti ayambe kugwira ntchito yawo. +Chomwe boma la DPP lapanga, ndi kuwalonga mafumuwa kuti ayambe kugwira ntchito komanso kuwaika pamndandanda woti ayambe kulandira mswahara, adatero Nankhumwa, pocheza ndi Tamvani pafoni. +Nankhumwa wati boma la DPP lakweza mafumu awiri okha omwe ndi Ngolongoliwa ndi Toleza koma ena onse adakwezedwa ndi Banda. +Ma Paramount amalandira K50 000, Senior Chief K30 000, T/A K18 000, Sub T/A K8 000, magulupu K5 000 ndi nyakwawa K2 500. +Nankhumwa akuti pakadali pano K1.7 biliyoni ndiyo ikugwiritsidwa ntchito kulipirira mswahara wa mafumuwa ndipo wati ndi kuonjezereka kwa enaku kupangitsa kuti ndalamazi zifike pafupifupi K2.5 biliyoni. +Izi zikudza pamene maunduna ena ofunika monga a zamaphunziro ndi zaumoyo alandidwa ndalama zina kupangitsa kuti maundunawa alephere kulemba aphunzitsi ndi anamwino ena. +Yemwe amathirira ndemanga pa nkhani zaumoyo ndi zipatala, Martha Kwataine, komanso kadaulo pa ndale Henry Chingaipe adzudzula izi ndipo ati kulibwino ndalamazi zipite maunduna. +Dziko lino lili pampanipani wa zachuma, zomwe zachititsa kuti boma lichepetse ndondomeko ya zachuma ndi K23 biliyoni chifukwa chomanidwa thandizo ndi maiko amene akhala akulithandiza. +Nankhumwa adavomereza akuti ndalama zomwe ziyambe kupita kwa mafumuwo ndi zambiri ndipo zidakathandizadi maunduna ena amene ali pampanipani monga unduna wa zaumoyo komanso wa zamaphunziro. +Timanenedwa ndipo mafumuwo amati mwina sitikuwapatsa malipiro chifukwa adakwezedwa ndi boma la Peoples Party (PP). Ndiye taona kuti nkofunika kuti tiwaike pamndandanda woti azilandira mswahara kuyambira tsopano, adaonjeza Nankhumwa. +Apapa zidalakwika kale ndiye sitingachitire mwina. Inde tilibe ndalama, koma nanga tikadatani? Chifukwa izi zikadapereka mavuto ena achikhala kuti tidawasiya kuti mafumuwo asamalandire [mswahara]. +Mafumu ena ayamba kale mwezi wathawu kulandira mswahara wawo malinga ndi ganizo la boma lowaika pamndandandawu. Mafumu 20 akwezedwa kale mwezi wa February mchigawo cha kummwera. +Koma Kwataine akuti boma lidziwe kuti kulakwitsa kuwiri sikungabweretse mayankho kwa anthu, ndipo yati boma likadaganiza kawiri. +Anthu akusowa mankhwala ndi zakudya mzipatala ndiye boma likuchotsa ndalama ku unduna wa zaumoyo kukapatsa mafumu? Boma litaunikapo bwino pamenepa, adatero Kwataine. +Iye adati sikulakwitsa kusiya kaye kukweza mafumu bola nthambi zina zinthu zikuyenda bwino malinga ndi mavuto a zachuma omwe dziko lino likukumana nawo pakalipano. +Anthu akulipa nkhuku ndi mbuzi kubwalo la mfumu, kodi zimenezi si zokwanira kwa mafumuwa? Ngakhale kuwasiya osamawapatsa ndalama palibe vuto chifukwa malipiro awo amapezeka kumudzi komweko. +Panopa mmidzi anthu akungophana pena kumenya anthu okalamba kusonyeza kuti anthu adataya chikhulupiriro mwa mafumu. Ndiye palinso chifukwa chowapatsira ndalama zambiri ngati zimenezi? adafunsa Kwataine. +Naye Chingaipe wati kulakwika kudachitika ndi boma la PP komabe boma la DPP likadaona nthawi yochitira izi. +Si zobisa, dziko lino lili pamavuto a zachuma, ndiye nchifukwa chiyani boma laganiza kuti achite izi lero pamene zinthu sizilibwino? Panopa mafumu akukhudzidwa ndi ndale, nchifukwa chake ndikufuna kuti bwanji boma laganiza zowaika pa mndandanda wolandira ndalama mafuwa lero? adatero Chingaipe. +Mneneri mu undunawu, Muhlabase Mughogho wati ntchitoyi sidayambe lero ndipo ili mkati mpaka mafumu otsalawa atathananawo. +Sitinganene kuti mafumu otsalawo tithananawo liti koma ntchito ili mkati, adatero mneneriyu. +Iye adati mafumu 41 900 ndi amene akhala akulandira mswahara mwa mafumu 42 150 amene ali mdziko muno, kusonyeza kuti mafumu 250 ndi amene sadayambe kulandira. +Mafumu amene akwezedwa mwezi wa February ndi T/A Nchiramwera wa ku Thyolo; Senior Chief Ngolongoliwa ya mboma la Thyolo; Senior Chief Kuntaja wa mboma la Blantyre; Senior Chief Kanduku ya mboma la Mwanza; T/A Ngowe ya mboma la Chikwawa komwe ufumuwu waima kaye pamene nkhani yapita kubwalo. +Ena amene akwezedwa ndi T/A Ndamera ya mboma la Nsanje; Sub T/A Toleza ya mboma la Balaka; Sub T/A Phalula ya mboma la Balaka; ku Machinga kuli Sub T/A Sale, T/A Nkoola, T/A Nkula, kudzanso Sub T/A Lulanga ndi Mtonda a mboma la Mangochi. +Chigawo chapakati ndi kumpoto kwakwezedwanso mafumu 11 ndipo ena akwezedwa miyezi ikudzayi. +Woganiziridwa kuba khanda anjatidwa ku Mzuzu Mayi wina zake zada mumzinda wa Mzuzu atamugwira ataba khanda la psuu la mnzake pachipatala chachikulu cha Mzuzu sabata yatha. Koma make mwanayo pano akumwetulira chifukwa khanda lakelo lilinso mmanja mwake! Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Wachiwiri kwa mneneri wa polisi ya Mzuzu, Cecelia Mfune, watsimikiza za kumangidwa kwa Mary Pundi Nyirenda, wa mmudzi mwa Chisi, T/ A Mpherembe mboma la Mzimba, yemwe akumusunga palimandi kundende ya Mzuzu komwe akudikirira kukaonekera kubwalo la milandu komwe akayankha mlandu woganiziridwa kuba khanda masiku akubwerawa. +Alinso limodzi: Wayisoni ndi mwana wake atapezeka Komatu khandali likadapita pakadapanda Maganizo Banda, mlonda wa kampani ya Stallion, yemwe ankalondera malowa usikuwo. +Banda adati adakhala tcheru ataona Nyirenda akutuluka ndi khanda kuchokera muwodiyo nthawi itatsala pangono kukwana 12 koloko usiku. +Mayiyu adatuluka katatu konse kulowera wodi ya amayi apakati, yomwe ili moyandikana kwambiri ndi wodi ya makandayi, atanyamula khanda lomwe adalikulunga mushawelo yoyera. Amati kutuluka nkulowa. +Apa ndidadziwa kuti china chake chasokonekera chifukwa kunja kudali kukuzizira ndipo mayi wanzeru sakadatuluka ndi mwana nthawi ngati imeneyo ndipo sindidamulole kuti atuluke, adatero Banda. +Pocheza ndi Msangulutso make khandalo, Mercy Wayisoni, wa zaka 27 yemwe amachokera ku Elunyeni mboma lomwelo koma kumudzi kwawo ndi kwa Nazombe, T/A Nazombe mboma la Phalombe, adafotokoza kuti adafika pachipatalapo Loweruka pa February 20 wopanda wina aliyense womudikirira. +Iye adati Loweruka lomwelo adakumana ndi mayi wina kukhitchini yemwe adamufunsa ngati ali ndi womudikirira ndipo iye atamuuza kuti adalibe aliyense womusamalira pachipatalapo, mayiyo adamupempha kuti akhale mnzake kuti aziphika ndi kudya limodzi osadziwa kuti adali zolowere nkudyere mwana. +Apa mpomwe ubwenzi wathu udayambira. Kwa masiku asanu ndi limodzi tinkadyera limodzi, adatero Wayisoni koma adati adadabwa kuti Lolemba nthawi yochira itakwana Nyirenda adamuletsa kuitana wachibale aliyense kuti amuthandizire ndipo adamuuza kuti wachibale aliyense asadziwe zoti nthawi yake yochira idali itakwana kaamba koti iye alipo ndipo amuthandiza. +Wayisoni adati Nyirenda adali kumutsatira kulikonse komwe amapita patsikuli mpaka kuchipinda cha opaleshoni komwe adanamiza adokotala kuti adali wolandirira mwana ngakhale adokotalawo adamuletsa kulowa mchipindamo. +Iye adati asadatuluke kuopaleshoniko, adokotala adamudziwitsa kuti adali ndi mwana wamwamuna. +Wayisoni adati adazizwa pomwe adadzidzimuka pakati pa usiku ndi kupeza kuti mwana wake salinso kumtima kwake koma mnzakeyo adali atamusunthapo. +Adandiletsa kumuyangana mwana wanga ndi kundiuza kuti khandalo silidali langa koma lake kaamba koti langa lidapitirira. Izi zidandikwiyitsa ndipo ndidauza oyandikana nawo kuti Nyirenda wanditengera mwana ndipo adasinthitsa nsalu ine ndili mtulo, adalongosola Wayisoni. +Iye adati nawo achipatala atamva kuti muwodimo mwauka mpungwepungwe adabwera ndi kutsimikiza kuti khandalo lidali la Wayisoni. +Flames itenga mwezi ikukonzekera Guinea Timu ya mpira ya dziko lino ya Flames itenga mwezi umodzi ikukonzekera masewero ake ndi Guinea omwe adzachitike mwezi wa March chaka chino mumpikisano wa Africa Cup of Nations. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Malinga ndi pulezidenti wa bungwe loyendetsa za mpira mdziko muno la FAM, Walter Nyamilandu, Flames idzayamba zokonzekerazi kumayambiriro a mwezi wa mawa. +Flames iyamba kukonzekera mwezi wa mawa Nyamilandu wati timuyi yapatsidwa mwezi umodzi yazokonzekera chifukwa osewera ambiri ali pa tchuthi malinga ndi kutha kwa ligi ya TNM Super League. +Monga mukudziwa tili ndi masewero akulu mu March chaka chino pomwe tikumane ndi Guinea. Potengera ndi zimene mphunzitsi watimuyi, Ernest Mtawali adapempha ku FAM, taona kuti nzofunika kuti tovomere zoti timuyo ikhale ikukonzeka nthawi yaitali. Paja osewera ambiri akupuma chifukwa TNM Super League yatha. Izi zikuonetseratu kufunika kotenga nthawi yaitali tikukozekera, adatero Nyamilandu. +Padakalipano, FAM yaloleza kuti mphunzitsi wa timu ya dzikolinoyo apite ku South Africa komwe akaunike ena mwa osewera a dziko lino kuti akhale nawo mutimu yomwe ikumane ndi Guinea. +Ena mwa osewerawa ndi Atusaye Nyondo yemwe amasewera mu timu ya Pretoria University ndi Robert Ngambi yemwe amasewera mu Platinum Stars amenenso ubale ndi Mtawali unada chifukwa sanalowetsedwe pomwe Flames imakumana ndi Swaziland chaka chatha. +Mmodzi mwa akatswiri a mpira mdziko muno Peter Mponda yemwe anali kaputeni wa Flames wayamikira FAM polola mphuzitsi wa timu ya dziko linoyo kupita kukaunika osewera omwe ali ku South Africa. +Iye watinso akadakonda kuti Mtawali akhalenso paubale wabwino ndi osewera ngati Ngambi chifukwa tchito zake ndizofunikirabe ku timuyi. +Mkangano uimitsa kumanga sukulu Njovu zikamamenyana umavutika ndi udzu, adatero akulu a mvula zakaale. Izi zapherezeka ntchito yomanga sukulu ya sekondale yoyendera ku Chombe mboma la Nkhata Bay itaima kwa zaka zisanu kaamba ka mkangano wa malo womwe unabuka mderalo pakati pa Gulupu Malepa ndi mwini munda womwe akufuna kumangapo sukuluyo, Michael Mkandawire. +Escom in free-for-all fuel scam Wait gets longer Secrecy over party funders Pomwe deralo lili ndi sukulu za pulaimale 11, lilibe sukulu ya sekondale, zomwe zikukweza chiwerengero cha ana osiyira sukulu panjira. +Anthu a mderalo ataona vutoli adapempha kuboma sukulu ya sekondale mchaka cha 2010. Motsogozedwa ndi mfumu yawo, Gulupu Malepa, adapeza malo pomwe adaumbapo njerwa kuti ntchitoyi iyambike. +Sichinga: Tili okonzeka kusamutsa njerwa Koma zinthu zidasokonekera pomwe zidadziwika kuti malo adaperekedwawo, udali munda wa Mkandawire, yemwe panthawiyo adali ku Dar es Salaam mdziko la Tanzania. +Mkandawire adauza Msangulutso kuti mchemwali wake ndiye adamuimbira foni kumudziwitsa kuti munda wake ukupita. +Iye adati izi zidachititsa abwerere kumudzi komwe adadzapeza zinthu zitavuta. +Ndidapempha kuti ngati akundilanda malowa, andipatse ena zomwe sizidatheke, koma chonsecho malowa ndi oti adatisiyira ndi agogo athu. +Pano akuti ndizipita kwathu ku Rumphi komwe sindikukudziwa chifukwa ndinabadwira konkuno mchaka cha 1972, nawo mayi anga adabadwiranso kuno mchaka cha 1950, adatero Mkandawire. +Iye adati chaka chino pamalopo sadalimepo chifukwa choospezedwa kuti atidzimulidwa. +Amfumu akufuna chitukuko chikhale pakhomo pawo, chifukwa akufuna adzakokenso magetsi sukuluyi ikadzabwera ndipo malo okhawo omwe apezeka ndi munda wanga, iye adatero. +A komiti ya chitukuko cha mmudzi village development committee (VDC) ya Malepa ataona mpungwepungwewu adapeza malo ena, koma mfumuyi ikukanitsitsa kuti sukuluyi ikamangidwe malo ena. +Malinga ndi wapampando wa komitiyi, Jefferson Sichinga, malo ena apezeka mdera la mfumu Malenga ndipo ndi okonzeka kusamutsirako njerwa zomwe zidaotchedwa pamalo akalewo. +Vuto ndi loti pachiyambi a gulupu adatisonyeza malo a mwini; nthawi yoti tiyambe chitukuko itakwana mwini wake adatulukira ndipo ngakhale tidagwirizana kuti timangapo timangoyenera kusuntha chifukwa mpamunda wa chinangwa wa mwini wake, adatero Sichinga. +Mkandawire: Akuti ndizipita kwathu Iye adati vuto lalikulu lomwe lilipo ndi loti Malepa akufuna chitukuko mkhonde mwake. +Malepa adavomereza zoti akufunadi chitukukocho chipite dera lake kaamba ka magetsi. +Eya. Zoonadi chifukwa ndine mfumu ya chitukuko, adalongosola Malepa. Iye adaonjezera kuti Sichinga yemwe ndi wapampando wa VDC akufunanso kuti malo a sukuluwo asinthe kaamba koti adasowetsa uvuni wa njerwa zokwana 100 000 ndipo akuthawa, nkhani yomwe Sichinga akuikana. +Polankhula naye pafoni Lachitatuli, Malepa adatemetsa nkhwangwa pamwala ponena kuti chitukukochi sichisuntha kaamba koti malo adaperekawa ali pakati pa derali. +Ine ndi a T/A Timbiri tikufuna sukulu ikhale pamalo omwe tidapereka mchaka cha 2010 pa Chombe Zion. Khansala wa dera lino Menson Simkonda ndiye akufuna kusuntha sukulu kuti ikhale kwawo ndi cholinga chodzawina mavoti mu 2019, adatero Malepa. +Iye adaloza zala khansalayo komanso wapampando wa VDC kuti ndiwo akumunyenga Mkandawire kuti akanize malowo. +Si malo a Mkandawire, koma akhansala ndi omwe akumpangitsa ndipo palowa ndale, pakufunika aboma komanso a Timbiri abwere tidzakhale pansi, adalongosola Malepa. +Iye adati sadalande Mkandawire malo. +Ngati ali malo ake apite kubwalo la milandu. Akadatisiyira malowo pano tikanakhala titamanga kale sukulu ndipo ana akuphunzirapo. Ine sindingalole ana azivutika kusowa sukulu chifukwa cha malo, idatero mfumuyo. +Koma khansala wa Mpamba Ward, Simkonda adati chomwe anthuwo akufuna ndi chitukuko. +Amfumu akufuna malo a munthu pomwe anthu aperekanso malo ena. Mfumu imodzi singapweteketse ana, adatero Simkonda. +Ndipo malinga ndi wampando wa VDC, katundu wa ndalama zokwana K12 miliyoni woti amangire buloko imodzi adabwerera masiku apitawa chifukwa aboma atafika kumalowo sadapeze malo oti nkusunga katunduyo. +Limodzi mwa mabungwe omwe akugwira ntchito mderalo kuchokera ku mpingo wa CCAP mu Sinodi ya Livingstonia, mthambi yake yoyangana za chitukuko ndi maufulu osiyanasiyana ya Church and Society, yati mderali mukufunika sukulu mwachangu. +Mmodzi mwa oyanganira pulojecti yomwe cholinga chake ndi kupereka mphamvu kwa anthu pa zitukuko pokweza ulamulilo wa ma boma angono Robert Ndovi adati zivute zitani, pofika September ana a fomu 1 akhale atayamba kuphunzira. +Ana ndi omwe akuluza chifukwa cha mkanganowu; anthu a dera lino angopeza nyumba zomwe zilipo kale kuti chaka chino maphunziro ayambe, adatero Ndovi. +Polankhulapo mkulu woona maphunziro mbomali Mzondi Moyo adati ofesi yake ikudziwa za kuchedwa kwa ntchito yomanga sukuluyi kaamba ka nkhani ya malo. +Mwini malowa adadandaula kuti ndi pokhapo pomwe amadalira ndi banja lake, ndipo malowo akatengedwa avutika, adatero Moyo. +Atuma anthu kupha Apolisi mboma la Chitipa atsekera mchitokosi bambo wina pomuganizira kuti adatuma achiwembu kupha mkazi wake wakale. +Facksoni Simbeye adatuma Filisoni Mbendera wa zaka 38 ndi bambo wina yemwe akungodziwika kuti Mshani kupha Lyness Mtawa, awiriwa atasemphana maganizo pankhani zina zambanja. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Malinga ndi mneneri wapolisi mchigawo cha kumpoto, Maurice Chapola, izi sizidamukomere Simbeye ndipo adakonza chiwembuchi pa 6 mwezi uno. +Maiyu adapezeka ataphedwa mmunda wa chimanga, koma atakhapidwa kwambiri mmutu, adatero Chapola. +Chapola adati anthu a mmudzi mwa Fyson Nyondo, T/A Mwabulambia mbomalo adatsatira mapazi kuchokera pomwe maiyu adaphedwera. +Mneneriyu adati apa mapaziwa adalunjika mnyumba mwa Mbendera, yemwe ataona khamu la anthuli adalikumba liwiro la mtondo wadooka. +Komabe adamugwira pomwe adaulula kuti Simbeye ndiye adawatuma kupha maiyu. Apatu anthu sadaugwire mtima koma adamtibula mpaka kumupha, adatero Chapola. +Ndipo mmodzi mwa anthu omwe amachokera mudzi umodzi ndi Mtawa koma adakana kutipatsa dzina lake adatsimikizira Msangulutso kuti Simbeye ndiye adakonza chiwembuchi kaamba ka ndalama za banki mkhonde. +Bamboyo adati ngakhale Simbeye adavomera atagwidwa ndi anthu a mmudzimo kuti ndiye adakonza upowo Banja lawo lidatha mwezi wa Novembala atakhala zaka zoposa zisanu, koma nkhani idagona pa K200 000 ya banki nkhonde yomwe mayiyo adatenga, adatero bamboyu. +Msika wa fodya utsekulidwa April Misika yaikulu ya fodya mdziko muno ikhoza kutsekulidwa sabata yachiwiri ya mwezi wa mawa, atero akuluakulu a bungwe lowona za fodya mdziko muno la Tobacco Control Commission (TCC). +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Fodya ndi mbewu yaikulu imene dziko lino limagulitsa kunja ndi kubweretsa ndalama zimene zimathandiza pa ntchito zina za boma. +Msika wa fodya wa okushoni Polankhula pa lamya kuchokera ku Lilongwe Lachiwiri, mkulu wa TCC Albert Changaya adati masikuwa ndiwongoganizira chabe popeza zokambirana zili mkati. +Apa Changaya adachenjeza alimi kuti misikayi ikatsekulidwa asamalitse ndi onyamula fodya ena omwe akumachita utambwali pobera alimi. +Iye adati onyamula fodya achinyengowa adabera alimi pafupifupi K1.4 biliyoni chaka chatha. +Ena mwa onyamula fodya amanama malo omwe atengako fodyayu ngati uli mtunda waufupi potchula dera lakutali ndi cholinga chofuna kuba. Kafukufuku yemwe adapanga akatswiri athu odziwa kulondoloza zachuma adapeza kuti mchaka chatha choka K1.4 biliyoni idapita, Changaya adatero. +Apa adanenetsa kuti anthuwa adziwe kuti kwawo kwatha chifukwa bungweli lili pa kalikiliki wokhazikitsa ndondomeko zatsopano zothana ndi mchitidwewu. +Tizigwiritsa ntchito nambala za zitupa za alimi zomwe pa Chingerezi timati zoning. Apa tizidziwa dera lomwe fodyayu akuchokera ndipo wonama aliyense azidziwika, Changaya adatero. Iye adati bungweli likukumana ndi onyamula fodyawa sabata yamawa kuti akambirane za ndondomeko zomwe zakhazikitsidwa pokonzanso zinthu. +Changaya adati TCC laletsanso bungwe limodzi kukhala loyanganira alimi lomwelonso lonyamula fodya. +Sabata zapitazi woyanganira kampani ya Auction Group mchigawo cha kumpoto, Joseph Kawinga adauza gulu la alimi akuluakulu a fodya ochokera mchigawocho kuti ena mwa onyamula fodya amatenga fodya kuchokera kwa alimi ndi kungomusiya mmalo osungira katundu mumzinda wa Mzuzu mmalo mokasiya kumsika wa fodya. +Kawinga adati chifukwa cha kukhalitsa kwa fodyayu mnyumbazi anthuwa amaluza ziphaso zoperekera fodya ndipo amakonzanso ziphaso zawo za bodza. +Mwamwayi ziphaso zabodzazi zomwe nambala zake sizigwirizana ndi nambala za pa zitupa zenizeni za kumsika wathu wa fodya, timazidziwa ndipo sitilola kuti fodyayu agulitsidwe popereka chiletso mpaka zonse zitalongosoka, adatero Kawinga. +Iye adapempha alimi kuti chaka chino ayesetse kupeza owanyamulira fodya okhulupirika oti akafikitsa mabelo awo kumsika wa fodya. +Mmodzi wa alimi akuluakulu a fodya mchigawochi Harry Mkandawire adati bungwe la TCC lichirimike pokonzanso ndondomekozi. +Boma libweza moto pa zolipiritsa mzipatala Ganizo la boma loyambitsa mbali yolipiritsa mzipatala zonse za boma kuyambira July akubwerayu, lalephereka, nduna ya zaumoyo, Peter Kumpalume, yatero. +Izi zikutanthauza kuti zipatala za boma mmaboma zikhalabe zaulere, monga zakhala zikuchitikira.Zitamveka kuti boma likufuna kuyambitsa mbali yolipiritsa mzipatala zonse za boma, anthu ena, mafumu komanso amabungwe sadasangalale ndi mfundoyo ndipo adapempha boma kuti lisayerekeze kubweretsa chilinganizochi. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Koma ngati kubwezera madzi kumkobwe, Kumpalume pano wati muunduna wake mudalibe ganizo lofuna kukhala ndi mbali ina yolipitsa mzipatala, mawu omwe akutsutsana ndi zomwe mneneri wa undunawu, Adrian Chikumbe, adauza Tamvani sabata zitatu zapitazo. +Nkhaniyi ikungokambidwa koma mosatsatira bwino mutu wake. Monga ndikudziwira, muunduna wanga mulibe ganizo lotere, adatero Kumpalume pouza nyuzi ta Weekend Nation ya Loweruka lapitali. +Kalata yosayinidwa ndi mabungwe monga Oxfam, ActionAid, Save the Children, Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR), National Association for People Living with HIV and Aids in Malawi (Napham), Medicines Sans Frontiers (MSF) and Development Communication Trust (DCT) idandauza boma kuti ganizo lokhala ndi mbali yolipitsa ivulaza anthu osauka. +Timothy Mtambo wa CHRR, adati anthu ovutika apitirira kuvutikabe chifukwa kumbali yaulere kukhala kopanda zipangizo zokwanira poyerekeza ndi kolipira. +Chidwi chizikhala kwa anthu olemera osati osauka, apa ndiye kuti osauka apitirira kusaukira, adatero Mtambo, ganizoli litangoululika. +Lero Mtambo ndi wokondwa kuti boma lasintha ganizoli. +Iyi ndi nkhani yabwino, pakutha pa zonse, ovutika adakakhala anthu ovutikitsitsa. Apa ndiye kuti zili bwino, adatero pothirapo ndemanga pa ganizo la boma losintha maganizo ake. +Likwata: Amuna aimba ngoma, amayi navina Likwata ndi mmodzi mwa magule amene amavinidwa pakati pa Ayao. BOBBY KABANGO adali mboma la Chiradzulu mmudzi mwa Njeremba kwa T/A Mpama komwe adapezerera gule wa likwata, yemwe ena amamutcha kuti namkwakwala. Uyutu ndi gule amene amavina amayi komanso atsikana. Kodi uyu ndi gule wanji? Nanga adayamba liti? Mtolankhani wathuyu adakokera pambali mayi amene amatsogolera guleyu. Adacheza motere: Eee! Wefuwefu ameneyu kutopa kumene? Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Hahaha! Padalitu ntchito pamene paja. Si maseweratu kuvina gule ameneyu chifukwa akafika pakolasi timayenera tidzipinde basi. +Tidziwane kaye. +Ndine mayi Idesi Chiwaya, ndipo ndipo ndimatsogolera gululi. +Kodi ndi gule wanji ameneyu? Ameneyu ndi gule wa namkwakwala, ena amati likwata. +Cholinga cha guleyu nchiyani? Kusangalatsa anthu basi. Timavina tikasangalala monga zachitikira leromu kuti tangosangalala ndiye tidakumana kuti tivine basi anthu adyetse maso. +Muli akazi okhaokha bwanji? Ameneyu ndi gule wa amayi, nchifukwa chake simudaonemo mwamuna kupatula awiri amene akutiimbira ngoma. +Ndaonamonso tiasungwana, timeneti timaloledwanso kukhala mgulumu? Eya, amenewo ndiye eni gululi chifukwa ife takulatu ndiye timakhala nawo kuti Mulungu akatitenga iwowo ndiwo adzatsogolere gululi. Sitikufuna kuti gule ameneyu adzafe. +Kodi guleyu saphunzitsa zoipa? Zoipa zanji? Ayi, ameneyutu ntchito yake ndi kusangalatsa anthu basi. +Simukuona kuti guleyu angapangitse kuti tianamwali tija tisodzedwe mwachangu? Hahaha! Musandiseketse inu, amene aja ndi adzukulu anga. Ndimawayanganira ndipo palibe angachite zopusa ndi ana amenewa. Akukula mmanja mwanga. +Dzina limeneli lidabwera bwanji? Dzina la guleli? Liti lomwe mukukamba? Ndikukamba la likwata Ndi dzina basi, kusonyeza gule wachikhalidwe pamene ena amati gule wa namkwakwala. +Chifukwa chiyani kulipatsa dzina la likwata? Basi, nawonso makolo adakonda kuti apereke dzinali. +Si zolaula zimenezi? Nanga mpaka likwata? Ayi, palitu maina a anthu ambirimbiri mdziko muno omveka ngati akulaulanso, kodi ndiye kuti anthuwo amachita zomwe dzinalo limatanthauza? Ife mukanena kuti likwata timatanthauza kuti ndi gule wosangalatsa basi. +Kodi ndi gule wa chikhalidwe chiti cha anthu? Uyu ndi gule wa Anyanja. Ambiri akhala akunena kuti ndi wa Alhomwe, koma zoona zenizeni ndi zomwe ndikunenazi. +Mavinidwe a guleyu andimaliza, tafotokozani momwe muchitira pamene mukuvina Ngoma ija ikamalira, ife timavina moitsatira uko tikuimba nyimbo zathu. Ndiye ikafika pakolasi, timachita ngati tikudumpha uko tikudula chiuno. Apa ndiye timagwadirira pansi ndi kuvina momatembenuka koma kumatembenuka ndi maondo kwinaku tikugundana ndi matako. Aka ndiye kavinidwe kake. +Adakuphunzitsani ndani? Makolo athu. Ineyo makolo anga ankavina kwambiri ndipo atamwalira ndidapitiriza mpaka kupeza amayi anzanga. Tonse tilipo 10 kuphatikizapo ndi abambo a ngoma takwana 12. +Abambo savina nawo chifukwa chiyani? Aaa! Inuyo mungakwanitse zomwe timachita zija? Eetu, nchifukwa timavina amayi okha. +Mudayamba liti kuvina guleyu? Chaka ndiye sindingakumbuke koma ndimakumbukira kuti panthawiyo ndidali ndi zaka 33. Pano zaka zanga ndidaziiwala koma zaposa 50. +Mumavina nthawi yanji? Timavina masana, moti nthawi zambiri timavina pazochitika monga pamisonkhano. Tavinirapo mtsogoleri wakale Bakili Muluzi komanso Bingu wa Mutharika. +Atsogoleriwa amakwanitsa kuduka mchiuno chonchi? Ayi, amangochoka pampando ndi kumavina pangonopangono ndipo mapeto ake amapisa mthumba kutipatsa kangachepe. +Kodi momwe munavinira apamu ndiye kuti mumathera pamenepa? Ayi, apatu tangovina kwa mphindi 5, koma tikati tivine moposera mphindi zimenezi mudakaona momwe timachitira. +Malangizo kwa amene satsatira gule wa makolo Amenewo azikhala pafupi ndi makolo awo kuti asataye chikhalidwe cha makolo awo. +Mlonda wosolola solar akwidzingidwa Pamene kampani ya Inovantis mboma la Machinga imanyadira kuti izigona tulo tabwino chifukwa yalemba ntchito Ibrahim Justin, wa zaka 23, ngati mlonda woteteza katundu wawo ku ndipsi, kampaniyi sinadziwe kuti yatuma galu kumalondera nyama ya mbuzi yowotcha kale. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Wojambula wathu akuganiza kuti zidali chonchi mukhoti Wapolisi wotengera milandu kukhothi pa Liwonde Police Post, Ezekiel Kalunga, adauza bwalo la milandu la Liwonde kuti pa April 19 chaka chino akuluakulu a kampani ya Inovantis adakagwada kupolisi kukadandaula kuti chipangizo chopanga mphamvu ya magetsi kuchokera kudzuwa (solar panel) chidasowa pakampanipo. +Kafukufuku woyangana chipangizochi ali mkati mkulu wa alonda pakampanipo adakumana ndi munthu wina atanyamula chipangizocho, chimene adachizindikira kuti ndi cha kampani yawo. +Alonda onse adatengeredwa kupolisi ndipo atapanikizidwa ndi mafunso kuti adazembetsa chipangizocho ndani, Justin adavomera kuti ndiyeyo adasolola. +Kalunga adapempha khothi kuti limuthyape Justin ndi chilango chachikulu popeza khalidwe lakelo ndi lothawitsa anthu, makamaka a maiko akunja monga Inovantis, kudzakhazikitsa bizinesi zawo mdziko muno. +Popereka dandaulo, Justin adapempha bwalo kuti limupatse chilango chochepa popeza iye ndi nsanamira ya banja lake. +Ziweto zisasowe mtendere mkhola yengo ya mvula ino, ziweto monga ngombe, mbuzi, nkhosa ndi nkhumba zimasauka kaamba ka matope mkhola, zomwe zimachititsa kuti ziwetozi zizisowa mtendere. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Nthawi zambiri ziweto zomwe khola lake limadikha, zimakhala zofooka nthawi zonse poti zimalephera kupuma mokwanira kaamba kakuti zimagona choimirira chifukwa cha chidikhacho. +Ngombe sizingapeze mtendere mkhola ngati ili. Ngakhale mkakawo ungakome? Mkulu woyanganira za ulimi wa ziweto ndi kuchulukitsa ziwetozo, Dr Ben Chimera, wati mchitidwe ngati umenewu umabwezeretsa ulimi wa ziweto mmbuyo chifukwa nthawi zina ziweto zimatha kugwidwa ndi matenda. +Pocheza ndi Uchikumbe, Chimera adati zoterezi zimachititsanso kuti mmalo monenepa, chifukwa msipu wamera, ziweto zimayamba kunyentchera kaamba koti mmalo moti zizidya, zimakhalira kugona kubusa. +Zimadabwitsa kuti mmalo moti ziweto zizinenepa poti msipu wamera, zikunyentchera. Chifukwa chake sichikhala china, ayi, usiku zimakhala kuti zachezera chiyimirire ndiye masana zimafuna kugona pamalo ouma mmalo momadya, adatero Chimera. +Iye adati ulimi wabwino wa ziweto nkutsatira zomwe amanena a zamalimidwe pakakonzedwe ka khola la ziweto komwe kamathandiza kuti nthawi zonse mkhola muzikhala mouma ndi mwaukhondo. +Pali njira zosiyanasiyana koma njira yosaboola mthumba ndi yomanga khola pamalo otsetsereka kuti madzi asamadekha mkhola. Ziweto zili ngati anthu, nazonso zimafuna malo abwino kuti zizitakasuka, adatero Chimera. +Mkuluyu adati kwa alimi a ziweto monga mbuzi ndi nkhosa, khola labwino ndi lammwamba kuti ndowe zizigwera pansi komanso madzi asamakhale mkholamo. +Chimera adati mlimi akhoza kumanga khola labwino pogwiritsa ntchito mitengo, luzi ndi tsekera ngati palibe ndalama zokwanira kugulira zitsulo ndi malata koma chachikulu nchakuti mkholamo muzikhala mouma. +Apa mutha kuona chomwe timalimbikitsira kubzala mitengo mmunda ndi pakhomo chifukwa sungavutike kokapeza mitengo yomangira khola, kungofunika kugula pepala lofolerera, basi kwinaku nkugwiritsa ntchito luzi, adatero Chimera. +Malingana ndi chimera, ziweto zokhala mkhola laukhondo zimadya mosangalala ndipo mpovuta kugwidwa ndi matenda ndipo zimaonekera bweya bwake kusalala kuti ndi zaukhondo. +NGAMBA IOPSEZANSO CHAKA CHINOUNDUNA Chaka chatha kudali kakasi pankhani ya ulimi mvula itadula pomwe mbewu zambiri, maka chimanga, zimamasula ndipo izi zidachititsa kuti alimi ambiri asakolole mokwanira moti pano ena njala idalowa kale. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Vutoli lidagwa kaamba ka mvula ya njomba, makamaka potsatira kusintha kwa nyengo, ndipo unduna wa zamalimidwe, mthirira ndi chitukuko cha madzi wachenjeza kuti zomwe zidaoneka chaka chatha zingathe kuchitikanso chaka chino mmadera ena. +Mlimi kudandaula ndi kufota kwa mmera mmunda chaka chatha Undunawu wati potengera zomwe apeza a nthambi ya zanyengo, madera ena akhoza kulandira mvula yokwana pomwe ena ayi ndipo izi zikhoza kuchititsa kuti mvula idzadule msanga mmadera ena. +Polingalira kuti alimi ambiri amadalira ulimi wa mvula, undunawu wati alimi amalize msanga kukonza minda yawo kuti mvula ikangogwa adzabzale mbewu ndi mvula yoyambirira. +Pali chiyembekezo chakuti madera ena akhoza kulandira mvula yochepa, zomwe zingapangitse ngamba mkati mwa nyengo ya mvulayi komanso zikhoza kupangitsa kuti mvula isiye msanga, chidatero chikalata chomwe udatulutsa unduna wa malimidwe sabata yathayi. +Undunawu wati pofuna kuthana ndi vuto ngati lomwe lidaoneka chaka chatha mvula itadula mosayembekezera, alimi amalize kukonza minda yawo mwachangu. +Undunawu watinso alimi alingalire kubzala mbewu zocha msanga komanso atsatire njira ya kasakaniza ndi njira zamalimidwe zamakono zosunga nthaka, chinyontho ndi chonde monga kuphimbira nthaka. +Undunawu watinso pomwe ntchito zakumunda zikuyenda, alimi akangalikenso nkukolola madzi kuti ngati mvula ingadzadule mdera lawo, adzakhale ndi madzi okwanira a mthirira komanso omwetsa ziweto. +Polingalira za chakudya cha ziweto mtsogolo muno, undunawu wati alimi omwe ali ndi ziweto akumbukire kubzala nsenjere ndi mitundu ina ya udzu chinyezi chikakhathamira mnthaka kuti asadzavutike nyengo ya chilimwe. +Tikufuna alimi atsatire zimenezi kuti udindo wathu woonetsetsa kuti mdziko muno muli chakudya chokwanira ukwaniritsidwe. Chaka chatha alimi adadzidzimutsidwa chifukwa sadayembekezere zomwe zidachitika. +Si kuti tayamba izi chifukwa cha phunziro la chaka chatha, ayi. Tidayamba kalekale kulimbikitsa alimi kuti azikonzeka nthawi yabwino nkumadikira mvula kuti ikangogwa azithamangira kumunda kukabzala, adatero mlembi wamkulu muundunawu, Erica Maganga. +Boma likonzekera el ninochilima Boma lati alimi ndi anthu mdziko muno asanjenjemere ndi lipoti la nthambi ya zanyengo loti chaka chino kukhoza kukhala mphepo ya El Nino ponena kuti zikachitika ilo ndi lokonzeka kuthana ndi mavuto amene angadze. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Saulos Chilima, adalengeza posachedwapa pamsonkhano wa atolankhani pofuna kupereka chilimbikitso kwa alimi ndi anthu onse. +Chilima:Boma litumiza alangizi ndi achitetezo mmadera osiyanasiyana Takhazikitsa thumba la ndalama zokwana K1 biliyoni zoti zitithandize kukonzekera mphepo imeneyi kuti isadzaononge, adatero Chilima. +Chilima adati ndalama zomwe boma lakhazikitsazi ntchito yake nkudzalimbana ndi mavuto monga kusefukira kwa madzi kapena ngamba zitati zachitika potsatira mphepo ya El Nino yomwe ikumvekayi. +Iye adati pokonzekera El Ninoyu, boma litumiza alangizi ndi achitetezo mmadera osiyanasiyana kuti mphepoyi itati yafika adzakhale athandizi a anthu populumutsa katundu ndi miyoyo ya anthu. +El Nino ndi mphepo yomwe imasokoneza ntchito za ulimi chifukwa chosapanganika. Nthawi zina mphepoyi imachititsa kuti mvula igwe yoononga pomwe nthawi zina imachititsa ngamba. +Mneneri wa unduna wa zamalimidwe Erica Maganga adati mvula ikagwa mopitirira muyeso, mbewu zimakokoloka pomwe kukachita ngamba mbewu zambiri zimalephera kucha. +Iye adati njira ziwirizi zimabweretsa vuto la njala ndi umphawi mdziko chifukwa anthu amakhala opanda chakudya ndi choti angagulitse kuti athandizike. +Chaka chatha mbewu zambiri zidakokoloka ndi madzi mvula itabwera moonjeza panthawi yochepa koma akatswiri adati izi sizidali zotsatira za mphepo ya El Nino koma kusintha kwa nyengo. +Mneneri wa nthambi yoona za nyengo, Sute Mwakasungula, wati anthu azitsatira zomwe nthambiyi ikunena pa mmene nyengo ikuyendera ndi kutsatira malangizo omwe nthambiyi ikupereka. +Iye adati mphekesera zina zomwe zimamveka pankhani yokhudza za nyengo zikhoza kusokoneza anthu, makamaka alimi omwe amakhala ndi nkhawa kuti mpamvu ndi zipangizo zawo zikhoza kupita pachabe. +Nthambi yathu ili ndi akatswiri omwe amadziwa momwe nyengo ikhalire ndipo amapereka malangizo a zomwe anthu angachite kuti asakhudzidwe kwambiri. Anthu azitsatira zimenezi, adatero Mwakasungula. +Afa atamwa bibida wosadyera Mneneri wa polisi ya Nkhotakota Williams Kaponda watsimikiza kuti bambo wina kumeneko wakabzala chinangwa atapapira mowa osadyera. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kaponda adati malinga ndi achibale, Damson Wasiya, 34, malemuwo omwe ndi Francis Phiri adapita kukapopa mowawo Lamulungu pa 8 November mbomalo. +Achibalewo auza apolisi kuti malemuwa adapezeka usiku akuchokera kopopa mowawo ali lamba! Mumsewu, zomwe zidakhudza ofuka kwabwino amene adamutengera kunyumba. +Ataona kuti mbaleyo akuoneka moti samapeza bwino, adathamangira naye kuchipatala cha boma komwe madotolo adakatsimikiza kuti adali atafa, adatero Kaponda yemwe adati zotsatira za achipatala zidaonetsa kuti malemuwo adafa chifukwa chomwa wosadyera. +Wofuna kugulitsa alubino achimina Bwalo la milandu la Mzuzu majisitireti lalamula Philip Ngulube, wa zaka 21, kuti akakhale kundende ndi kukagwira ntchito yakalavulagaga kwa zaka 6 atamupeza ndi mlandu wofuna kuba msungwana wachialubino ndi cholinga chofuna kumupha. +Ngulube, yemwe adali mphunzitsi wodzipereka pasukulu yapulaimale ya Mongo mboma la Mzimba, adagwirizana zomanga banja ndi msungwanayo, wa zaka 17, yemwe ankaphunzira pasekondale ya Mzimba. +Escom in free-for-all fuel scam Wait gets longer Secrecy over party funders Ngulube (akukokera kabudulayo) kutuluka mkhoti ulendo wa kundende Koma mphuno salota, Ngulube adali ndi maganizo ogulitsa msungwanayo kwa munthu wajohn chirwa malonda yemwe ndi mbadwa ya mdziko la Tanzania. +Koma msungwnayo adapulumukira mkamwa mwa mbuzi mbadwa ya ku Tanzaniayo itakatsina khutu apolisi za malonda omwe Ngulube adali nawo. Apolisi ndi luntha lawo, adapita kwa Ngulube ngati ofuna kugula mualubinoyo. +Apa mpamene Ngulube adakwidzingidwa ndi unyolo zitapezekadi kuti amagulitsa mtsikana wachikondi wakeyu pamtengo wa K6 miliyoni. +Nkhani idapita kubwalo la majisitireti Gladys Gondwe komwe adazengedwa mlandu wofuna kuba munthu ndi cholinga chofuna kumupha, womwe adaukana. +Koma Lolemba lapitali, Gondwe muchigamulo chake chomwe chidatenga mphindi zisanu zokha, adalamula kuti Ngulube akagwire gadi kwa zaka zisanu ndi chimodzi. +Gondwe adati mlandu womwe amazengedwa Ngulube uli ndi chilango cha zaka zisanu ndi ziwiri. +Iye adati adaganiza zopereka zaka 6 ndi cholinga chakuti Ngulube adziwe kuipa kwa mchitidwe wofuna kuba munthu. +Woweruzayu adati nzomvetsa chisoni kuti msungwanayo adasiya sukulu chifukwa cha kusowa mtendere ndi zomwe adachita Ngulube. Iye adati izi nzotsutsana ndi malingaliro a mabungwe ndi boma polimbikitsa maphunziro a asungwana. +Wozenga mlandu wamkulu kuchigawo cha kumpoto, Christopher Katani, adati ndi wokondwera ndi chigamulo chomwe bwalo la milanduli lidapereka. +Iye adati zaka 6 ndi zokwana potengera kuti mlandu womwe amazengedwawo umayembekezereka kulandira chilango cha zaka 7. +Katani adatinso ndi wokhurira poti nkoyamba kumpoto bwalo lamilandu kutumiza munthu kugadi chifukwa cha mchitidwe wakuba anthu achialubino. +Ngulube polandira chilangochi, adaoneka kuti adali woyembekezera matherowo chifukwa sadaoneke kudodoma kulikonse. +Boma liganizire bwino pa sabuside Adzavutika: Nkhalamba ndi ana amasiye Mkonzi, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndalemba kalatayi kutsatira zomwe nduna yoona zaulimi a Allan Chiyembekeza adanena masiku apitawa. +Mukunena kwawo, a Chiyembekeza adati boma likufuna kuti anthu omwe angalandire mbewu ndi fetereza zotsika mtengo chaka chino asalandirenso chaka chinacho. +Iwo akuti izi zithandiza kuthetsa mchitidwe wa chinyengo komanso kuchepetsa mchitidwe woti anthu amodzimodzi ndi amene azipindula mundondomekoyi. +Adzavutika: Nkhalamba ndi ana amasiye Ngakhale maganizo amenewa akuoneka ngati abwino, ine ndikuona kuti mfundoyi ipweteketsa magulu ena a anthu. +Ndikunena izi chifukwa boma silidatiuze ndondomeko zomwe liike pofuna kuonetsetsa kuti okalamba ndi ana amasiye omwe amalerana okhaokha omwe sangathe kudzigulira feteleza ndi mbewu pamsika liziwathandiza bwanji. +Palinso anzathu omwe ali ndi mavuto osiyanasiyana monga kulumala omwe akhala akudalira feteleza ndi mbewu zotsika mtengo kuti apeze kachakudya kokwanira timisiku tingapo kudzera mu ulimi. +Awa ndi ena chabe mwa magulu a anthu omwe sangathe kudzigulira mchere wamnthaka ndi mbewu pamsika pomwe thumba limodzi la feteleza panopo ndi cha pakati pa K22 000 ndi K23 000. +Choncho, ndikufuna ndifunse boma kudzera kwa a Chiyembekeza kuti litiuze ndondomeko yomwe lakonza poonetsetsa kuti anthu akuthandizika pamene boma likugwiritsa mfundo yoti munthu yemwe wapindula chaka chino asadzapindulenso chaka chinacho. +Khrisimasi ya maluzi Kwangotsala masiku anayi kuti chisangalalo cha Khrisimasi chifike pachimake koma ochita bizinesi zosiyanasiyana akudandaula kuti sizikudziwika kuti nyengoyi yafikadi malingana ndi momwe akuvutiramalonda. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ochita malonda mmisika ikuluikulu ya mmizinda ya Mzuzu, Lilongwe ndi Blantyre ati pomafika nthawi ngati zino mzaka zammbuyomu, bizinesi zawo zimayenda kwambiri moti ena amapikula katundu kawiri kapena katatu pasabata, koma chaka chino akuti zimenezo kulibeko. +Ngakhale msitolo zikuluzikulu monga za Shopright malonda sakuyenda kwenikweni Anthu ena omwe adapikulira katundu mwezi wa November mpaka lero akadagulitsa yemweyo, malonda akuvuta. Zoti ndi December malonda amayenda ayi ndithu, osadziwika nkomwe, adatero Mlembi wa ochita malonda mumsika wa mzinda wa Mzuzu Justin Hara pocheza ndi Tamvani Lachitatu. +Iye adati momwe zikuonekera, anthu alibe ndalama kapena ndalama ali nazo koma akuopa kuti akazisakaza adzavutika, malingana ndi momwe chuma chikuyendera. +Tikuganiza kuti ambiri akulingalira za mafizi akwerawa komanso akuti akaona momwe chuma chikuyendera akuda nkhawa kuti akadya ndalama adzakhala pamavuto aakulu. Magulitsidwe ake akungokhala ngati talowa kale January, adatero Hara. +Wa pampando wa msika waukulu mumzinda wa Lilongwe, George Banda, adati zikuoneka kuti chaka chino mumsika nzamalodza zomwe sizidachitikepo nkale lonse. +Malonda asanduka ngati muja amachitira a minibasi kuchita kuthamangira munthu kunjira kumukokera pamalonda, kutanthauza kuti bizinesi yafika povuta. Zikumatheka ena mpaka kuweruka momwe adabwerera ndithu, adatero Banda. +Mkuluyu adapereka tsatanetsatane wa momwe ochita malondawa amatcherera bizinesi zawo polinganiza katundu yemwe amakonda anthu akumudzi ndi apantchito zomwe adati sizikutheka chaka chino. +Timatchera kuti mwezi wa November timapikula zomwe amakonda anthu akumudzi ndipo timayembekezera kuti tikalowa December katundu ameneyu amakhala atatha chifukwa anthu ambiri akumudzi amadzaguliratu zinthu kuti azikagwira ntchito zina. +Tikamalowerera mkati mwa December, timakapikula za anthu apantchito mtawuni, koma pano ambiri tikadali ndi katundu woyambirirayo, adatero Banda. +Kaphidigoliyu sadasiye anthu a kummwera komwe akuti nako zinthu sizikuyenda momwe zimakhalira mmbuyomu. +Wapampando wa ochita malonda mumsika waukulu ku Blantyre, Himon Amanu, adati nyengo ngati ino mumsinkawu mumakhala gulu la mundipondera mwana, koma chaka chino anthu akuyenda mosacheukacheuka. +Zinthu zatembenukiratu, palibe chikuyenda. Anthu afumbata ndalama zawo ndipo sakufuna kuononga, ayi, adatero Amanu. +Zonsezi nchifukwa cha kuchepa mphamvu kwa ndalama ya kwacha. +Chaka chino chokha kuchoka mu March ndalama ya kwacha yagwa kuchoka pa K435 posinthanitsa ndi ndalama ya Amerika ya dollar kufika pa K612 mwezi uno wa December. +Kuchepa mphamvu kwa ndalamayi kwadza chifukwa chakuti dziko lino silikugulitsa malonda kumaiko akunja mokwanira. Kupatula fodya, shuga, tiyi, thonje ndi mbewu zina, palibe malonda omwe dziko lino likudalira kuti akhazikitse kwacha pansi. +Malingana ndi odziwa za chuma, mphamvu ya ndalama imakhazikika ngati dziko likupanga katundu wabwino yemwe maiko ena akumukhumba. +Dziko la Malawi limadalira mabungwe ndi maiko akunja omwe amapereka thandizo la ndalama, zomwe zimapangita kuti ndalama ya kwacha isakhale pendapenda. +Ndiye pomwe mabungwewa adati asiya kuthandiza dziko lino kaamba ka kusolola ndalama mboma, mavuto akhala aakulu mdziko muno. +Chinanso chomwe chikupangitsa kuti ndalama ya kwacha iguge ndi chakuti dziko la Amerika chuma chake chikuyenda bwino kwambiri, zomwe zapangitsa kuti ndalama ya dollar ikhale yamphamvu kuposa ndalama zina monga ndalama ya pound. +Izi zapangitsa kuti maiko ambiri osauka akhale pachiopsezo chifukwa chuma chawo sichikuyenda bwino. +Bungwe la International Monetary Fund (IMF) lomwe ndi limodzi la mabungwe omwe amathandiza dziko lino ndi ndalama, msabatayi lati dziko la Malawi liyenera kukhwimitsa ndondomeko ya zachuma chake kuti anthu osolola ndalama asiye. +Bungwelo latinso boma lichepetse kusakaza ndalama pazinthu za zii zopanda mutu, kuonjezera kuti boma likuyenera kuchitapo kanthu kuti zinthu zitsike mtengo poonetsetsa kuti pali mfundo zabwino zoongolera chuma. +Koma bungwe la amipingo la Public Affairs Committee (PAC) lati anthu asaiwale cholinga cha chikondwererochi poganizira zosakaza ndalama. +Wapampando wa bungweli, mbusa Felix Chingota, wati nyengoyi ndi yokumbukira kubadwa kwa mpulumutsi Yesu Khrisitu osati kungolingalira zonjoya basi. +Inde, ndi nyengo yachisangalalo anthu akuyenera kusangalala, koma asaiwale cholinga cha chisangalalocho chifukwa ena amapezeka kuti chisangalalo chomwecho avulala nacho mwinanso kutaya nacho moyo mmalo mopata moyo mwa Yesu Khrisitu, adatero Chingota. +Adzikonzera mpumulo wa bata Ukayenda umaona agalu a michombo ndithu. Ku Rumphi aliko oyenda masanasana pamene bambo wina wa zaka 62 wakumbiratu manda owaka bwino kuyembekezera tsiku lomwe Namalenga adzati kwatha. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Sasintha Mnozga, yemwe ndi mbusa wa mpingo wa African Church adakonza mandawa ndi ndalama zoposa K200 000 mmudzi mwa Mnozga, mfumu yaikulu Chikulamayembe mbomalo. +Koma mafumu mderali ndi wodabwa ndi mchitidwewu, zomwe akuti ndi zotsutsana ndi chikhalidwe cha Atumbuka pakuti munthu saloledwa kukumbiratu manda ake. +Mandawo ndi amenewa: Pali tsiku lakubadwa koma palibe lakufa Mnozga, pocheza ndi Msangulutso Lachitatu, adati sakuonapo vuto lililonse mwakuti pano akusakasaka makobidi ena kuti aguliretu bokosi lomwe adzamuyikemo akamwalira. +Ndikufuna kukonzeratu zonse kuti abale anga asadzavutike kusakasaka makobidi okonzera manda anga ndikadzamwalira. Abale anga ambiri ndi ovutika moti sangadzakwanitse kugula ngakhale bokosi, adatero Mnozga yemwe ali ndi ana 10. +Iye adati china chomwe chidamuchititsa kuti akumbiretu manda ndi momwe anthu salemekezera maliro kumanda. +Anthu amangoponya dothi pamwamba pabokosi ngakhale litakhala la makobidi ochuluka bwanji. Izi sizimandisangalatsa konse. +Mandawa ndawakonza ndi miyala komanso matumba 11 a simenti. Izi zikutanthauza kuti bokosi langa silidzakhunzana ndi dothi monga mmene zimakhalira mmanda ena, adatero Mnozga. +Mnozga amachitanso bizinesi pa boma la Rumphi. Ali ndi chigayo komanso malo ogonapo alendo. Iye adali mfumu kumudzi kwawo koma adasiyira mwana wawo atayamba ubusa mchaka cha 2001. +Pamene adayamba kukumba mandawa mchaka cha 2013, abale awo adawakaniza koma iwo adakakamirabe. Poyamba ankakana koma nditawalongosolera chifukwa chomwe ndimachitira izi adavomera mosasangalala momwemo. +Koma kwa mafumu silidali vuto chifukwa adali anzanga paja nane ndidali mfumu, adatero Mnozga. +Mfumu yaikulu Chikulamayembe, yomwe idati idawaonapo mandawa, idakana kulankhulapo pankhaniyo. +Koma mfumu Kayiwale Chirambo ya mderali idati zomwe adachita Mnozga sizololedwa pa chikhalidwe chawo. +Pachikhalidwe chathu sitivomera munthu kukumbiratu manda ake. Koma vuto ndi lakuti masiku ano anthu ali ndi ufulu ochita zomwe akufuna. Pachifukwa ichi, mpovuta kuti timuletse, adatero a Chirambo. +Iye adati sakudziwa chomwe chidachititsa Mnozga kubwera ndi ganizo lotereli. +Ife sitikudziwa kuti kaya ndi misala, kaya ndi uKhristu kapena chuma. Tonse ndife odabwa, koma palibe chomwe tingachitepo chifukwa chakuti ndi ufulu wake kutero. +Koma kukanakhala kwakale tikadawaitanasa nkuwaletsa kuchita zimenezi. Atati akana tikadatha kuwalanga, adatero Chirambo. +Mnozga siwoyamba kudzikumbira manda mbomali. Pa Mzokoto padalinso a SS Ngoma yemwenso adazikumbira manda. Koma atamwalira abale awo adakhaniza zokawayika kwina ndi komwe adamanga mandawo. +Asanamwalire, mtsogoleri wakale wa dziko lino Bingu wa Mutharika adakonzeratu nyumba yomaliza yomwe adagonamo iye ndi mkazi wake Ethel. Mandawo amatchedwa Mpumulo wa Bata. +Chidyaabusa: Nthumbwana yofewetsetsa Zamkati mwa nyama monga ngombe kapena mbuzi zija ena amati nthumbwana ndi ndiwo zofewa zomwe ambiri amakonda kupatsa mafumu kapena akuluakulu pakakhala mwambo wa zochitikachitika. Nthumbwanazi zimakhala ziwalo zosiyanasiyana za mkatimo ndipo pakati pa izo pamakhala chiwalo china chomwe anthu amakhulupirira kuti oyenera kudya ndi abusa oweta ziweto. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Vincent Kalimba zokhudza chiwalochi. +Kalimba kufotokoza za mwambo wa chidyaabusa Ndikudziweni Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndine Vincent Kalimba wa kwa Mbwatalika. Ndili pabanja ndipo ndimachita ulimi wa mbewu ndi ziweto. +Kodi kuno zolembana ntchito ya ubusa ziliko? Kwabasi ndipo anthu ambiri omwe ali ndi ziweto ali ndi antchito osamala ziwetozo. Pena zimatheka watchito mmodzi kumasamala ziweto za anthu angapo bola ngati akukwanitsa kulongosola pokazilowetsa mkhola madzulo zikakhuta. +Ndikhulupilira nthumbawana mumazidziwa, kodi ndi chiyani? Nthumbwana ndi zamkati mwa nyama monga ngombe kapena mbuzi. Zimakhala zofewa kwambiri bola zikaphikidwa bwino ndipo nthawi zambiri amadya ndi mafumu kapena akuluakulu pakakhala mwambo. +Zimakhala ziwalo zanji? Ndi ziwalo zosiyanasiyana monga mtima, matumbo, mafuta, chifu, mphafa, chiwindi, kapamba ndi mapapo. +Ndiye pazomwe mwatchulazo amati palinso chidyaabusa, chimenechi chimaoneka motani? Chimakhala ngati chija ena amati chibulangete kapena bafathaulo koma chimasiyana chifu poti chidyaabusa chimakhala chofewa kwambiri moti nthawi zina amatha kudya chachiwisi. +Zidatani kuti chikhale chidyaabusa? Ndi dzina lomwe makolo kalelo adapereka potengera kuti eni ziweto akapha mbusa amamupatsa nthumbwana imeneyo kuti akadye. Mchitidwewu udazolowereka moti olo mwini ziweto aphe zingapo, mbusa amatenga nthumbwana zimenezozo. +Malipiro ake amakhala chidyaabusacho basi? Ayi, amatha kumpatsanso nyama ina monga momwe mwini wakeyo waonera koma samalephera kumupatsa chidyaabusacho. +Nanga poti ena amati nthumbwana zimayenera kuperekedwa kwa mafumu kapena alendo ngati ulemu? Nzoona, koma chidyaabusacho amatenga ndi osamala ziweto. Mafumu ndi alendo amawapatsa nthumbwana zinazo. Nzosachitanso kubisalira poti olo mafumu amadziwa kale mwambo umenewu. +Padalibe tanthauzo lapadera lochitira izi? Padalibe kungoti kumakhala ngati kumulemekeza wosamalayo komanso zimamupangitsa kulimbikira pantchito yakeyo. Abusa ena amatha kunyanyala ngati chiweto chaphedwa koma osaona chidyaabusa. +Kunyanyala kwake kumakhala kotani? Pena umatha kudabwa kuti dzuwa lakwera koma khola likadali lotseka. Kufufuza umangomva kuti mbusa wako watsegulira makola ena nkudupha lakolo ndiye umangodziwa kuti akulonjerera chidyaabusa cha chiweto chomwe udapha. +Ndiye kukambirana kwake kumakhala kotani? Kukambirana basi monga anthu. Mwina kungopepesana ndi mawu ngati mumamvana kapena kumpatsa mazira a nkhuku kapena ndalama kuti apitirize ntchitoyo. +Limakhala pangano polembana ntchitoyo? Ayi ndithu, koma kuti zidangokhala ngati mwambo wake kuti mbusayo azilandira nthumbwana imeneyo ndipo ambiri amangootcha nkudya osatinso kudikira zokaphika kunyumba. +Bwanji mabwanawo samangomusiya wonyanyalayo nkulemba wina? Ziweto nzovuta kwambiri, makamaka ngombe ndi mbuzizo. Ena amakhulupirira kuti khola limatengera mutu wa mbusa ndiye kusinthasintha abusa nthawi zina kumasokoneza mphumi. Komanso pali ngombe zina zomwe zimazolowera mbusa wawo moti akasintha zimakhoza kuchita ukali. Nchifukwa pena mumaona kuti mbusa watsegula khola koma ngombe zina sizikutuluka. +Kwaterera kwa ntenje Mwanunkha mmudzi mwa Ntenje kwa T/A Machinjiri mboma la Blantyre komwe osungitsa chitetezo mmidzi (community police) adatibulidwa nkumangiriridwa pamtengo kumanda komwekonso adawakumbitsa manda. +Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Kuonjezera apo, apolisi omwe amati akasungitse bata kumeneko adabwerako akulikumba la mtondo wadooka, kuthawa anthu okwiya, malinga ndi Gulupu Ntenje wa deralo. +Mmene timalemba nkhaniyi nkuti achitetezo a mmudzimu akubisala mtchire pamene ena akulandira chithandizo pachipatala cha Limbe. +Akulephera kukhala chifukwa chovulazidwa mmatako: Story Ntenje, yemwe nkhaniyi idachitika mmudzi mwake, adati izi zidachitika pamene anthuwo amaganizira kuti achitetezowo adapha munthu. +Gulupuyu akuti lidali Lachinayi pa 1 October pamene mmudzimo anthu ankathamangitsa mnyamata wina amene amamuganizira kuti waba thumba la chimanga kwa agogo ake. +Anthu adamugwira ndipo adayamba kumumenya. Achitetezo cha mmudzi ndiwo adamulanditsa kuti asavulazidwe. Adakamutsekera muofesi ndipo adaimbira apolisi ya Bangwe kuti adzamutenge, adatero Ntenje. +Iye adati pamene nthawi imakwana 4 koloko madzulo, apolisi adali asadafikebe. +Adatiuza kuti alibe mafuta. Kenaka poti tikamuone munthuyo tidapeza kuti wamwalira, adatero Ntenje. +Lamulungu pa 4 October, mwambo wa maliro udayamba, koma khamu la anthu ammudzimo akuti lidayamba kunena kuti a achitetezo a mmudzi ndiwo adapha malemuyo. +Mmodzi mwa achitetezowo, Davie Story, adati anthuwo adafika kunyumba kwake namugwira cha mma 8 koloko mmawa. +Adandigwira kuphatikizaponso anzanga ena awiri amene timagwira nawo ntchito ya chitetezo cha mmudzi. Adatitengera kwa wapampando wathu, koma tidakapeza atcheyawo atathawa. Ndiye adatenga mkazi wawo. +Adatitengera kumanda komwe adatikumbitsa manda. Titamaliza adayamba kutikwapula nkutimangirira pamtengo, adatero Story. +Ntenje adati panthawiyo, iye adaimbira apolisi kuti abwere. Apolisiwo akuti adalipo anayi ndipo atafika kumandako anthu okwiyawo adayamba kunola zikwanje kuti athane nawo. +Zinthu zidavuta, ndipo adaitana apolisi ena. Atafika enawo, tidayesera kukamba ndi anthu okwiyawo kuti awamasule pamtengo achitetezowo, zomwe zidatheka, adatero Ntenje. +Koma akutsitsira mmanda bokosi la maliro, mphekesera idamveka kuti anthuwo amafuna kuti achitetezowo awaponyere mdzenjemo nkuwakwiriria limodzi ndi chitandacho. +Story, amene akukanika kukhala pansi chifukwa cha kuvulazidwa mmatako, adafotokoza malodzawo motere: Adati tonse anthu 5 tigone limodzi ndi malemuwo. Amati atiponyera mdzenjemo. Zitavuta, apolisi adayamba kutithawitsira komwe adaimika galimoto yawo. +Ntenje adati apolisi adathira utsi wokhetsa misozi komabe sizidaphule kanthu ndipo adatha phazi kusiya mmudzimo muli chipwirikiti. +Apa mpamene anthuwa adapita kukagwetsa ofesi ya achitetezowo komanso kukayatsa nyumba ya wapampando wawo kuphatikizapo nyumba ya Story. +Wapampandoyo, Damiano Dindi, amene adalankhula pafoni ndi Msangulutso kuchokera ku Nsanje, komwe amati akubisala, adati palibe chomwe wapulumutsa mnyumba mwake. +Akazi anga ali mmanja mwa apolisi komwe akutetezedwa; mwana wanga wapita kwa achibale; ineyo ndili mtchire pansi pa mtengo wa bulugama mboma la Nsanje. Sindikudziwanso kuti ndi mmudzi mwa ndani, adatero Dindi. +Kolowera kwandisowa. Mutu wanga sukugwira chifukwa mnyumbamo mudali K280 000 ya bizinesi komaso katundu wanga yense wapita. +Mneneri wa polisi ya Limbe, Pedzisai Zembeneko, adatsimikizira Msangulutso za nkhaniyi ndipo adati womwalirayo dzina lake adali Nyadani Dankeni. +Koma Zembeneko adati kafukufuku pankhaniyi adali mkati ndipo adzalankhula zambiri akamaliza zofufuza zawo. +Pakalipano palibe amene wamangidwa kaamba ka kumwalira mwadzidzidzi kwa Dankeni kapena, adatero mneneri wa polisiyu. +Chilango chowawa kwa wogulitsa nyama ya galu Bwalo la majisitireti la Balaka lapereka chilango chowawitsa kwa mkulu amene wakhala akugulitsa nyama yagalu kwa zaka 14. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Pamene gawo 181 la zilango mdziko muno, limene apolisi adamangira Ishmael Jumbe, limati wolakwira lamulolo akhale kundende miyezi itatu kapena kulipira chindapusa cha K50, wogamula Victor Sibu adati mkuluyo akakhale kundende chaka chimodzi. +Malinga ndi mneneri wa polisi ya Balaka Joseph Chadwala, woweruzayo sadapereke mwayi woti Jumbe nkupereka chindapusa. +Asanagamule, Jumbe adapempha bwalolo kuti limupatse chilango chocheperako chifukwa anthu amene adawadyetsa nyamayo adamukhululukira kale. Iye adatinso ali ndi ana atatu amene amadalira iye, adatero Chadwala. +Jumbe: Galu amakoma ngati nyama yambuzi Koma Sibu adati chifukwa adaonetsa kuti ili ndi khalidwe lake kugulitsa nyama yagalu pempho lake silidamveke. +Polankhula ndi Msangulutso ali mmanja mwa apolisi Lachitatu lapitali, Jumbe adati wakhala akugulitsa nyama yagalu kwa zaka 14 ndipo adaiyamba mumzinda wa Blantyre ku Mbayani pomwe amakazinga nyamayo pamalo otchedwa Chiimirire. +Jumbe, yemwe ndi wa mmudzi mwa Kangaude kwa T/A Nkaya mboma la Balaka, adanjatidwa Lamulungu pa 15 November pamene makasitomala ake adamupeza akusenda galu. +Pomwe ndinkayamba izi, ndidali ndi mnzanga, timagulitsira pa Chiimirire komanso mmalo omwera mowa. Ndidali ndi makasitomala ambiri amene amakonda bayabaya, adatero Jumbe, amene akuti ankakonda kugulitsa kanyenya wa nyama ya galuyo madzulo. +Iye adati mosakhalitsa mnzakeyo adamwalira, zomwe zidamuchititsa kuti apite ku Balaka komwenso adakapitiriza bizinesiyo. +Sinditola agalu akufa, ndimachita kugula wamoyo nkumupha ndekha. Galu amene andigwira nayeyu ndidagula pamtengo wa K1 000. Uyuyu ndiye ndidamuphera panjira chifukwa atandigulitsa, amavuta kuyenda. Ndidamupha ndi kumumangirira panjinga. +Kunyumba ndimafika cha mma 12 koloko usiku ndipo ndidangofikira kumusenda. Mmawa ndidamuphika mchidebe, kenako ulendo wakumsika wa Njerenje kukagulitsa, adatero Jumbe. +Iye adati chomwe amataya akapha galu ndi mutu ndi mapazi komanso chikopa koma zammimba zonse amaphikira kumodzi. +Mutu ndi zipalapasiro [mapazi] komanso chikopa ndi zomwe ndimachotsa. Zammimba ndi ziwalo zina timaphikira kumodzi. Uyuyu adali wofula ndiye adali wamafuta kwambiri moti chidebecho adachita kumata mafuta okhaokha, adatero. +Titamufunsa ngati iye adayamba wadyapo galu, adati ndi nyama yabwino ndipo zikadakhala bwino nyamayi ailoleze kuti izigulitsidwa poyera. +Momwe imamvekera nyama yambuzi ndi chimodzimodzi ndi nyama yagalu. Yofewa komanso yamafuta. Ena amati nyama ya galu imawawa koma nzabodza, iyi ndi nyama yokoma ndipo ine ndidayamba kalekale kudya, adatero Jumbe. +Ndipo ikangofika pamsika simachedwa kutha, aliyense amafuna abaye basi. Ziwaya za anthu ena zimapezeka sizinathe koma ine chatha kale mmaola awiri okha. +Iye adati atakagulitsa nyama ya galuyo, Loweruka mmawa kudalawirira anthu kunyumba kwake kukamufunsia za nyama yomwe adawadyetsayo. +Iwo amati adamva mwana akunena kuti adandiona ndikusenda galu. Ndidakana powayankha kuti idali nyama ya mbuzi. Kenaka atavuta ndidawauza zoona ndipo adanditengera kwa mfumu. Mosakhalitsa ena adadziwitsa apolisi omwe adabwera kudzandimanga. +Ndikungopempha kuti andikhululukire ndipo sindidzachitanso. Andimvetse chifukwa agalu amene ndimagula amakhala abwinobwino, bola akadakhala achiwewe bwezi ili nkhani ina, adaonjeza. +Mmodzi mwa anthu amene adabaya nawo nyama yagaluyo koma sadafune kutchulidwa, adati sadazindikire kuti idali ya galu. +Ndidalibe chidwi kuti ndimvetsere bwinobwino pamene ndimadya, basi ndidangoti ndi nyama yambuzi. Koma nditangomva zoti adali galu, ndidadziguguda ngati ndisanze komabe sizikadatheka, adatero. +Anthu 7 amene adadya nawo nyamayo adawatumiza kuchipatala cha Balaka kuti akawaunike, koma onse awatulutsa, malinga ndi Chadwala. +Lamulo lochotsa mimba ladengula Akufuna ogwiriridwa, opatsana pathupi pachibale ndi ana achichepere aziloledwa kuchotsa pathupi Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Lamulo lokhudza kuvomereza kuti amayi akhoza kumachotsa mimba movomerezeka latsala pangono kupita ku Nyumba ya Malamulo kuti aphungu akalikambirane, Msangulutso watsinidwa khutu. +Mlangizi wa mmene ntchitoyi ikuyenera kuyendera kubungwe lomwe likulimbikitsa kuti boma livomereze kuchotsa mimba popanda mlandu la Coalition on Prevention of Unsafe Abortions (Copua), Luke Tembo, wati kukonza lamuloli kudatha kale ndipo kwatsala kuti aphungu akalikambirane. +Tidasiya nkhaniyi mmanja mwa nthambi ya zamalamulo (Law Commission) kuti aunike lamulo lomwe lidalipo kale ndipo tikunena pano lamulo lina lidatha kale kukonzedwa ndipo likungodikira kupita ku Nyumba ya Malamulo, adatero Tembo. +Wothandizira ntchito zounika malamulo kuthambi ya zamalamulo, Mtamandeni Liabunya, Lachisanu adatsimikiza kuti nthambiyi idamalizadi kukonza lamulo latsopanoli ndipo kwatsala kuti liyende mundondomeko zina lisadasindikizidwe. +Zonse zoyenerera zidachitika kale ndipo tidamaliza, pano tikungoyembekezera kuti tikatule kuunduna woona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa amuna ndi akazi komanso chisamaliro cha ana kuti ndondomeko izipitirira mpaka ku Nyumba ya Malamulo, adatero Liabunya. +Nduna yoona kuti pasamakhalae kusiyana pakati pa amuna ndi amayi komanso chisamaliro cha ana, Patricia Kaliati, adati unduna wake sukudziwapo kanthu pa za lamulo latsopanoli. +Kaliati: Sitingalole zimenezo Iye adati ali ndi njala yoona lamulolo kuti aone ngati zomwe zilimo zikugwirizana ndi zolinga za boma pa za tsogolo ndi moyo wa amayi ndi asungwana. +Nkhaniyitu okhudzidwa kwambiri ndi amayi ndi asungwana ndiye ife ngati unduna wa boma, sitingalole chilichonse chomwe chikusemphana ndi mfundo za boma zotukulira amayi ndi atsikana. Atipatse tilione lamulolo ndipo tiliunike, adatero Kaliati. +Bungwe la Copua likulimbikitsa zobweretsa lamulo latsopanoli pofuna kuchepetsa imfa za amayi ndi asungwana komanso ana chifukwa cha njira zochotsera mimba zamseri poopa kuti kuchipatala sakaloledwa komanso angaimbidwe mlandu wofuna kupha. +Tembo adati lamulo lakale limangolola munthu kuchotsa pathupi pokhapokha ngati pali umboni wakuti moyo wa mayiyo kapena mwana uli pachiopsezo. Koma lamulo latsopanoli laonjezerapo zifukwa zina zochotsera mimba. +Lamulo latsopanoli lawonjezera zifukwa zina zomwe munthu angathe kuchotsera mimba, monga mimba yobwera kaamba kogwiriridwa; mimba yopatsana pachibale; mimba zopatsana ana [osakhwima pamchombo]; komanso amisala aziloledwa kuchotsa mimba, adatero Tembo. +Kaliati adati unduna wake sugwirizana ndi ganizo lovomereza kuchotsa mimba kaamba kakuti uku nkuphwanya ufulu wa mwana wosabadwayo. +Iye adati akudziwa zoti magulu ena akulimbikitsa zokhazikitsa lamulo lovomereza kuchotsa pakati, koma boma lidanena kale poyera kuti kuteroko nkusokeretsa mtundu wa Amalawi, makamaka asungwana. +Kodi kuuza anthu uti akhoza kumachotsa mimba mmene afunira ndiye kuti tikumanga dziko lanji? Zimenezi zikhoza kuchititsa kuti anthu, makamaka asungwana, atayirire podziwa kuti akatenga mimba akachotsa, adatero Kaliati. +Iye adati boma limangovomereza lamulo lomwe lilipo pakalipano lomwe lidayamba kuonetsa mphamvu mchaka cha 2010. Lamuloli limalola munthu yemwe moyo wake uli pachiwopsezo kuchotsa pathupi. +Wapampando wa komiti ya aphungu achizimayi mNyumba ya Malamulo, Jessie Kabwila adati komitiyi iyambe yaona lamulo lomwe lapangidwalo ndi mfundo zake. +Tione kaye mfundo zomwe zili mulamulolo nkukambirana chifukwa mukomiti mumakhala anthu amaganizo osiyanasiyana. Ena amakhulupirira kuti kuchotsa mimba nkupha pomwe ena amazitengera paufulu wa anthu ndiye mpofunika titagwirizana chimodzi ngati komiti, adatero Kabwira. +Iye adati kupatula kusemphana maganizoku, nkhani yochotsa mimba njofunika kuyiona bwino chifukwa amayi ambiri akutaya miyoyo yawo tsiku ndi tsiku kaamba kochotsa mimba. +Mneneri wa polisi mdziko muno Rhoda Manjolo adati imfa zokhudzana nkuchotsa mimba zikuchuluka akatengera mmabuku a kupolisi. +Iye adati malingana ndi kafukufuku wa polisi, ambiri mwa amayi ndi asungwana omwe amachotsa mimba amachita izi kaamba ka mantha kapena kukhumudwitsidwa ndi omwe adawapatsa mimbazo. +Malamulo a ukwati akutsutsana Kutanthauzira lamulo lokhudza maukwati a ana kukhala kovuta tsopano pamene pali kusemphana pakati pa zomwe zidalembedwa mmalamulo oyendetsera adziko lino ndi zomwe zili mmalamulo okhudza mabanja la Divorce and Relations Act. +Gawo 22 ndime 6 ya malamulo a dziko lino limati palibe munthu woposa zaka 18 adzaletsedwe kukwatira kapena kukwatiwa. Ndime 7 imati munthu wa zaka pakati pa 15 ndi 18 angathe kukwatiwa kapena kukwatira ngati patakhala chilolezo kuchoka kwa makolo kapena womuyanganira. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Izi zikusemphana ndi zomwe zili mu lamulo latsopano loyendetsera maukwati zoletsa ukwati wa munthu wosaposa zaka 18. +Ku Dedza, T/A Kachindamoto akuchotsa mafumu amene apezeka akuvomereza ukwati wa mwana wosaposa zaka 18. +Mwa chitsanzo nyakwawa Galuanenenji idachotsedwa pampando chifukwa chovomereza ukwati wa mtsikana wa zaka 15 ngakhale makolo ake adavomereza kuti ukwatiwo uchitike. +Kachindamoto akuti mphamvu akuzitenga mu malamulo oyendetsera maukwati momwe akuletsa ukwati wa mwana wosaposa zaka 18. Tsono kuti tichotse mfumu pampando, malamulo amenewa tidachita kugwirizana tokha kuno ndiye mfumu yomwe yalakwitsa ikuchotsedwa ndipo mafumu anayi achotsedwa, adatero Kachindamoto. +Koma Esmie Tembenu wa Blantyre Child Justice Magistrate akuti pali kusokonekera kwazinthu chifukwa cha Divorce and Relations Act. +Chifukwa cha ubwino woti ana kuti azipita kusukulu, lamulo la maukwati ndi lomwe tikugwiritsa ntchito komabe tili ndi mantha chifukwa izi si zomwe zili mmalamulo adziko lino. +Ngati wina atakutengera kubwalo la milandu, angathe kukapambana mlandu chifukwa malamulo adziko lino okha ndiwo ali ndi mphamvu, adatero Tembenu. +Naye mphunzitsi wa za malamulo kusukulu ya Chancellor College Edge Kanyongolo akuti pamenepa pali kusokonekera kwa zinthu komabe wati lamulo la dziko lino ndilo lili ndi mphamvu. +Masiku apitawa, Kanyongolo adati pofuna kugwiritsa zomwe zili mu lamuloli, ndiye pakuyenera kukonza gawo 22 lomwe lili mmalamulo adziko lino. +Kudali kosungitsa ndalama Ena ukamalowa mbanki amangoganiza kuti chaphindu chochoka mmenemo ndi kusunga kapena kutapa ndalama komatu ena akusimba lokoma chifukwa tikukamba pano ali pa banja lokoma. +Sadock Ngambi wa ku Chitipa yemwe amagwira ntchito yoonkhetsa chuma kubungwe la Unesco akuti amakaika ndalama za bungweli kubanki ndipo mwamwayi adakumana ndi Tumenye Mwenitete wa ku Karonga yemwenso amakasungitsa ndalama. +Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Awiriwa akuti adakhala pa mzere umodzi mbankimo ndipo amacheza ngati adadziwana kalekale apo kudali kukumana kwawo koyamba mwinatu chilankhulo chidagwilapo ntchito. +Mpaka imfa kudzawalekanitsa: Sadock ndi Tumenye Adandisangalatsa momwe adamasukira nane ndipo mumtima ndidangomva kuti tseketseke. Mmene amamwtulira, timanyazi pangono ndi sangala ndidaona ndekha kuti koma mkazi ndi uyu, adatero Sadock. +Iye adati panthawiyo mchaka cha 2010 sadathe mawu adangopempha nambala ya lamya ya mmanja yomwe adalandira naye nkupereka yake ndipo kuyambira apo udali ubale ochezerana pa lamya. +Ataona kuti bobobo amuzulitsira boonaona adalimba mtima nkupita kukaonekera kwawo kwa Tumenye ndipo monga mwa mwambo wa kwawo adapereka malowolo nthawi yomweyo kuti ena asowe khomo lolowera. +Nditapereka malobolo, padapita chaka china ndipo mchaka cha 2012 ndi pomwe tidamanga woyera ku Kawale CCAP ndipo madyerero ake adali kusukulu ya sekondale ya Chipasula, adtero Sadock. +Iye adati akaona mkazi wakeyo amakhala ngati waona makolo ndi abale ake chifukwa cha chikondi ndi chisamaliro chomwe amalandira. +Naye Tumenye sadafune kuotcha chofunda koma kuyamikira ndi kuthokoza kuti adapeza mwamuna wakukhosi kwake. +Ambiri alipo okwatira ndi kukwatiwa koma ineyo pandekha ndimadzitenga wodala. Mwinanso ena amadzitenga odala mmaanja awo ndiye kuti nawo adapeza wawo ngati mmene ndidapezera wanga, adatero Tumenye. +Tikunena pano awiriwa ndi bambo ndi mai aulemu wawo, opemphera komanso okondana ngati mkazi ndi mwamuna. +Akufuna mayankho pa njala ya mzipatala Mabungwe omwe si aboma ku Rumphi ati akudikirabe yankho kuchokera kwa mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika pa zakusowa kwa chakudya mzipatala zosiyanasiyana mdziko muno. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mwezi wathawu, mabungwe omwe ali pansi pa Civil Society Network ku Rumphi adachita zionetsero ngati njira imodzi youza boma kuti lichitepo kanthu pa zakusowa kwa chakudya pachipatala cha Rumphi. +Banda kuwerenga chikalata chomwe adalembera boma Mabungwewa adauza Mutharika, kudzera mchikalata chomwe adapereka kwa akuluakulu a boma, kuti awayankhe pasanadutse sabata ziwiri. +Wotsogolera mabungwewa, Eunice Banda, wauza Tamvani kuti boma silinayankhebe chikalata chawocho. +Iye wati mabungwewa akufuna kukhalanso pansi kuti apeze njira ina yopezera mayankho kuchokera ku boma. +Titachita zionetsero boma lidapereka matumba 100 a chimanga. Koma chakudya chimenechi chitha kumapeto a mwezi uno. Izi zikutanthauza kuti kukhalanso njala kuyambira mwezi wamawa, adatero Banda. +Nduna ya za masewero ndi chikhalidwe, Grace Chiumia, masiku apitawa adauza mabungwe kuti achepetse zionetsero chifukwa chakuti boma limamva kamodzi. +Chiumia, polankhula ku Nkhata Bay pamene amakhazikitsa ntchito zolimbana ndi nkhanza mbanja, adati ndalama zomwe mabungwe akugwiritsa ntchito pazionetsero azipititse kuntchito zachitukuko. +Boma lisavomereze kuchotsa pathupi Potsatira zomwe ndinalemba sabata yatha, mmodzi wa awerengi watumiza maganizo ake motere: Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Rabecca, Ndine mmodzi mwa amene ndimatsatira zimene umalemba patsamba ili ndipo sindinagwirizane ndi maganizo omwe udalemba sabata yatha kuti ndi bwino malamulo a dziko lino alole amayi omwe akufuna kuti azitha kuchotsa pakati mzipatala. +Ndikudziwa pali mavuto omwe akudza kaamba koti anthu akuchotsa pakati pogwiritsa ntchito njira zoopsa zomwe zikumavulaza kapena kupha amayi ndi atsikana, komabe yankho la mavutowa si kuvomereza kuti anthu azingotaya pakati mwachisawawa. +Ine ndimakhulupirira kuti moyo ndi mphatso ya mtengo wapatali yomwe Namalenga amapereka kwa munthu. Malembo amanenetsa kuti tisanabadwe kapena kuti munthu asanapangidwe nkomwe mmimba mwa mayi wake, Mulungu amakhala atamudziwa kale. +Kwa ine, izi zikusonyeza kuti pathupi paliponse pamapangidwa ndi Mulungu amene amapereka moyo, posaona kuti wotenga pathupiyo akadali pasukulu, wagwiririridwa kaya sadalowe mbanja. +Ndiye ngati Mulungu walola kuti woterewa akhale woyembekezera ndiye kuti amakhala ndi cholinga ndi moyo wa mwana akuyembekezeredwayo, choncho ncholakwika kuti mayiyo aloledwe kuti azichotsa moyowo. +Ngati chamukomera Mulungu kuti pakhale moyo, Mulunguyo amadziwa kuti mwana wobadwayo asamalidwa bwanji. Timaona anthu amisala akubereka ana nkumakula mmatauni ndi mmizindamu. Ngati munthu wamisala akutha kulera mwana, kuli bwanji anthu alungalunga? Mwina simunaonepo, koma ine ndikudziwa za ana ena omwe adabadwa makolo awo ali pasukulu kapena sadalowe mbanja, ndipo ndikamba pano anawa ndi anthu ofunikira omwe amapindulira dziko liko komanso kuthandiza makolo awo. +Izi zomati anthu azichotsa mimbazi zimangoyangana mavuto alero osaunikira kutsogolo komanso cholinga cha Mulungu pokulola kuti ukhale ndi pathupi. +Ndikudziwa kuti kutenga pathupi uli pasukulu kapena usanapeze banja zimaoneka ngati zolakwika, koma izi zisapangitse kuchotsa pathupi kukhala ngati ndi chithu cholungama. Ndine mayi Banda, Blantyre. +Tetezani kukokoloka kwa nthaka ndi biyo Njira zotetezera nthaka kumadzi othamanga zili mbwee, koma katswiri wa zanthaka kusukulu yaukachenjede ya Chancellor College, Dr Jimmy Namangale, wati kuika biyo mmalo momwe mumadutsa madzi ndi njira yabwino yopewera ngalande mmunda. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Polongosolera Uchikumbe sabata ino, katswiriyu adati mmalo momwe mumadutsa madzi, makamaka mmunda, zaka zikamapita mumasanduka ngalande kutanthauza kuti nthaka yomwe idali pamenepo idanka kwina ndi madziwo. +Iye adati mlimi akalekelera osachitapo kanthu, zotsatira zake munda umaonongeka komanso zimachititsa kuti mitsinje ndi madambo omwe amasunga madzi omwe akadagwira ntchito ya mthirira zikwiririke. +Biyo wopangidwa ndi miyala amateteza nthaka ku madzi othamanga Ili ndi limodzi mwa mavuto omwe alimi ambiri amalekerera koma ndi chifukwa chimodzi mwa zifukwa zomwe zabwezeretsa ulimi mmbuyo. Zimaoneka ngati palibe chomwe chikuchitika chifukwa chaka chilichonse gawo lochepa lokha la nthaka ndilo limapita. +Izi zimakhala zikuchitika chaka ndi chaka ndipo podzazindikira, mmunda mumakhala mutadzadza ngalande ngati mitsinje, adatero Namangale. +Katswiriyu adati njira yodalirika yopewera zoterezi nkuyika biyo mmalo momwe mumadutsa madzi kuti liwiro la madzi oyendawo lizichepa komanso biyo amathandiza kuwakha nthaka yomwe imayenda ndi madzi. +Paupangiri wake, iye adati biyo savuta kukonza kwake, koma nzoyenerera kufunsa upangiri wa alangizi pogwira ntchitoyi chifukwa pamakhalanso ukadaulo wapadera kuti miyala yopangirayo ilimbe, isadzakokoloke. +Biyo amateteza nthaka ku madzi oyenda, makamaka othamanga, monga mudziwa kuti masiku ano mvula ikangogwa pangono madzi amathamanga kwambiri chifukwa chosowa poimira malingana nkuti mitengo ndi chilengedwe zidatha, adatero Namangale. +Mkuluyu adati pokhapokha mavuto ngati awa atathetsedwa, ngozi zina ngati kusefukira kwa madzi ndi kukokoloka kwa mbewu zisanduka nyimbo ya chaka chilichonse komanso nthaka idzafika potheratu kutsala thanthwe basi. +Mogwirizana ndi zimene adanena Namangale, katswiri wina wa zanthaka ku Bunda, Dr Patson Nalivata, adati pomwe alimi akuyesayesa njira zosiyanasiyana zobwezeretsera chonde mnthaka, mpofunikanso kuti azitsatira njira zoteteza kukokoloka kwa nthakayo. +Iye adati palibe tanthauzo lililonse kuti chaka ndi chaka alimi azikhala ndi ntchito yokokera chonde mmanyowa koma osachiteteza kuti chisakokolokenso. +Atukuka ndi kukwatitsa mitengo ya zipatso Masiku ano nkhani ili mkamwamkamwa paulimi ndi yogwiritsa ntchito mitundu ya mbewu zamakono zomwe akatswiri adayesa nkupeza kuti zili ndi kuthekera kotukula ulimi. Alimi a zipatso nawo adayambapo kutsata nzeruzi ndipo ena akusimba lokoma. Alimi a gulu la Taweni Farmers Club ku Mzimba akuchita nawo ulimiwu ndipo akudalira kwambiri kukwatitsa mitengo ya zipatso. Wapampando wa gululi Jester Kalua adafotokozera STEVEN PEMBAMOYO za ulimiwu motere: Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mlimi pantchito yake: Kalua kukwatitsa mitengo ya zipatso Bambo, dzina ndani? Dzina langa ndi Jester Kalua wa mmudzi mwa Kamanga kwa T/A Mtwalo ku Mzimba. Ndine wapampando wa gulu la alimi la Taweni Farmers Club. +Kodi kalabu imeneyi mumapanga zotani? Ife timapanga ulimi wa zipatso zosiyanasiyana monga malalanje, mapapaya, mango, mapichesi ndi mapeyala. Tili ndi malo aakulu kwambiri omwe timabzalapo mitengo yazipatsoyi ndipo timathandizana kusamalira ngati gulu. +Inu mumabzala mitundu yotani ya zipatsozo? Pali ntchito ndithu chifukwa sitimangofesa basi nkumayembekezera kuti tidzaokere, ayi. Pali zambiri zomwe timachita koma kwakukulu nkukwatitsa mitengo yathu yazipatso. +Mukutanthauzanji mukatero? Ndikutanthauza kuti timatha kufesa mitengo ina yomwe sivuta kumera nkusamala panazale koma kenako timaikwatitsa ndi mitengo ina yomwe imabereka bwino koma imavuta kafesedwe kake. +Kukwatitsako mumtani? Tikafesa mitengo yathu timayanganira mpaka itafika pamsinkhu wokwatitsa. Pokwatitsapo timadula nthambi ya mtengo womwe tikufuna kuti ukwatidwewo nkuikapo nthambi ya mtengo womwe tikufuna nkumanga. Tikatero timapitiriza kusamalira. +Ndiye mtengowo sungafe? Ayi. Zomwe timachita nzakuti sitidula nthambi zonse koma mwina imodzi nkusiya nthambi zina zoti zizipanga chakudya cha mtengowo uku ukugwirana ndi unzakewo. Zikagwirana bwinobwino timatha kudzadula nthambi zinazo kuti mtengo wokhawo womwe tikufuna upitirire kukula. +Cholinga chake nchiyani? Timafuna kupeza phindu lochuluka paulimi wathu chifukwa mbewu yomwe timaphayo imakhala yobereka pangono kusiyana ndi mbewu yokwatitsayo ndiye timafuna kupindulapo pa mbewu inayo. +Mungatchuleko mitundu ya mbewu zomwe mukukwatitsa pakalipano? Tikukwatitsa mandimu ndi malalanje, mango achikuda ndi achizungu komanso mapichesi achikuda ndi achizungu. +Ndiye mwati kusiyana kwake nkotani? Kusiyana kwake nkwakuti mbewu zachizunguzi zimabereka zipatso zikuluzikulu komanso zimabereka kwambiri kuposa mbewu zachikuda. +Koma sindikumvetsa pakakwatitsidwe ka mandimu ndi malalanje. Nchifukwa chiyani mumapha mandimu kuti mudzakolole malalanje? Pali zifukwa zingapo. Choyamba mandimu savuta kafesedwe kake poyerekeza ndi malalanje ndiye timafuna kuti mandimuwo atiyambire moyo wosavutawo kenako nkuupatsira ku malalanje. Chachiwiri, mandimu ndi malalanje chili ndi msika waukulu ndi malalanje ndiye munthu aliyense akamabzala mbewu zodzagulitsa amaganizira za msika choncho ife timaona chanzeru kulimbikira malalanjewo. +Mwanenapo za kasamalidwe, kodi mumasamala bwanji mitengi yanuyo? Zoonadi mitengo imafunika chisamaliro chokwanira bwino chifukwa kupanda kutero simungapeze phindu. Chiopsezo chachikulu ndi moto wolusa womwe umayamba mosadziwika bwino choncho mpofunika kulambula bwinobwino munkhalango ya zipatso. Kupatula apo mitengo sichedwa kugwidwa ndi matenda osiyanasiyana choncho pamafunika kuyendera pafupipafupi kuti ngati mwaoneka chizindikiro cha matenda, vutolo lithetsedweretu. +Nthawi yokolola mumatani? Choyamba sitingokolola chisawawa koma pamakhala nthawi yake yokololera ndipo timayamba taona ngati zipatsozo zafika poti tikhoza kukolola. Timakana kungokolola chisawawa chifukwa zipatso zokolola zanthete zimabweretsa maluzi chifukwa maonekedwe ake zikapsa amakhala osapatsa chikoka. +Inu misika yanu ili kuti? Tili ndi misika yosiyanasiyana ya zipatso. Zipatso zina timapikulitsa kwa mavenda ndipo zina timapita nazo mmagolosale akuluakulu omwe amatigulitsira nkumatipatsa ndalama. +GANIZO LOKWEZA FIZI LIBWERETSA NJIRIMBA Kudali matatalazi ku Nyumba ya Malamulo Lachinayi lapitali pamene aphungu adapindirana ndevu mkamwa pokambirana za ganizo la boma miyezi itatu yapitayo lokweza fizi msukulu zasekonadale ndi zaukachenjede mdziko muno ndipo sizikudziwika kuti aphule poto ndani pankhaniyi. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Nkhaniyi idatentha mNyumba ya Malamuloyi pomwe aphungu, maka otsutsa ndi oima paokha, adadzudzula boma kuti silidakhoze pokwenza fizi msukuluzi kaamba koti panthawi ino Amalawi ambiri ali pamavuto aakulu a zachuma malinga ndi njala yomwe yagwa mdziko muno. +Ngakhale mbali ya boma mNyumbayi idayesetsa kuti nkhaniyi isakambidwe, aphunguwo sadagonje mpakana mapeto ake adagwirizana kuti nkhaniyi ndi yofunika kuunikidwa modekha. +Adayambitsa nkhani: Jumbe Boma, kudzera muunduna wa zamaphunziro, lidakweza ndalama zolipirira maphunziro msukulu za boma zasekondale ndi zaukachenjede ati pofuna kuchepetsa chipsinjo chomwe boma lidali nacho poyendetsa sukuluzi. +Panthawiyo, mneneri wa unduna wa zamaphunziro Manfred Ndovie adati kukwera kwa fiziku nkopindulira Amalawi chifukwa zithandiza kuti maphunziro apite patsogolo. +Pali zambiri zomwe zikufunika kukonzedwa pankhani za maphunziro. Choyamba ndi malo ophunziriramo, zipangizo zophunzirira, malo ogona ndi chakudya. Kuti izi zisinthe mpofunika ndalama ndiye mukudziwa kale mmene boma lilili pankhani ya zachuma, adatero Ndovie. +Koma phungu wa chigawo cha pakati mboma la Salima, Felix Jumbe, yemwe ndi wachipani cha MCP, adati kukweza kwa fizi kwafika panthawi yomwe Amalawi ambiri ali ndi vuto la njala komanso mavuto a zachuma. +Iye adati zomwe boma lidaganizazi nkufuna kusautsa anthu osalakwa omwe ali kale paumphawi wadzawoneni. +Aphungu ambiri adagwirizana ndi ganizo la Jumbe ndipo mmodzi mwa iwo ndi Esther Jolobala woima payekha, yemwe adati zomwe adanena Jumbe ndi ganizo lozama lofunika kuliona bwino. +Ganizo lokweza sukulu fizi silidafike nthawi yabwino. Zimenezi zisokoneza makolo ambiri ndipo ine sindili muno kufuna kusangalatsa mbali ya boma kapena yotsutsa, koma anthu a kudera langa kummawa kwa boma la Machinga, adatero Jolobala. +Nduna ya zachilungamo ndi malamulo Samuel Tembenu idayesetsa kuletsa zokambirana nkhaniyi ponena kuti nyumba ya malamulo ilibe mphamvu yosintha lamulo kudzera mnjira yomwe Jumbe adatsata. +Naye phungu wa kummwera kwa boma la Mangochi, Lilian Patel, wa chipani UDF, adati nkhaniyo si yofunika kukambidwa kaamba kakuti sidali pamndandanda wa nkhani zofunika kukambidwa, koma sizidamveke ndipo zidatengera sikikala wa Nyumbayo Richard Msowoya kulamula kuti nkhaniyo ikambidwe ndi kuunikidwa ndi aphunguwo. +Pambuyo pake aphungu adagwirizana kuti boma lisakweze fizi panopo mpaka mtsogolomu zinthu zikayambanso kuyenda bwino kumbali ya chuma. +Potsirapo ndemanga, mkulu wa mgwirizano wa mabungwe oona kuti maphunziro akuyenda bwino la Civil Society Education Coalition (CSEC), Benedicto Kondowe, adati kukweza fizi nkofunika kuti maphunziro aziyenda bwino koma adati boma silidatsate ndondomeko yabwino. +Iye adati ndi mmene zinthu zilili panopa, anthu amafunika nthawi yokwanira kukonzekera osangoti lero ndi lero chifukwa Amalawi ambiri alibe ndalama. +Kunena chilungamo mMalawi muno muli mavuto. Omwe ali ndi ndalama ndi anthu ochepa kwambiri ndiye kukweza fizi panthawi yomwe anthu akukonzekera zaulimi si chanzeru. Akadayamba alengeza nkupereka nthawi yokonzekera, adatero Kondowe. +Lambani wadza ndi Knock Out Dzina la Limbani Banda, yemwe masiku ano amadzitcha kuti Lambanie Dube si lachilendo kwa otsata zoimba ku Malawi. Iye adatchuka zedi mmbuyomu ndi nyimbo yake ya Chisoni Nkumatenda ngakhalenso Kulira kwa Kholo. KONDWANI KAMIYALA adacheza naye kuti amve za chimbale chake chatsopano. Adacheza motere: Banda: Tithane ndi kupondelezana Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Chimbalechi chaphulidwa liti? Chimbale chatsopanochi, chotchedwa Knock Out chidatulutsidwa pa 22 October chaka chomwe chino. Ichi ndi chimbale changa cha nambala 11. +Knock out, ndiye kuti chiyani? MChingerezi, ndikhoza kumalizitsa kuti Knock out oppression, inde kuthana ndi kuponderezana. Tikuyenera kuthana ndi nsanje ndi nkhanza komanso zoipa zonse. +Choyenera kuchita nchiyani? Maganizo athu ayenera kusintha basi. Sitingatukuke ngati tikupita kusukulu ndi cholinga chodzalembedwa ntchito basi. Tiyenera kupita kusukulu ndi maganizo akuti tidzalembe ena ntchito patsogolo. Dziko likusintha ili. Kalelo munthu akakhala ndi galimoto zimakhala ngati ndiwolemera koma onani lero aliyense akudziwa kuti galimo nchinthu choti chimafunika pamoyo wa munthu kukhala nacho. +Kodi mchimbalechi muli nyimbo zingati ndipo zina mwa nyimbozo ndi ziti? Muli nyimbo 13 ndipo zina mwa nyimbozo ndi Stuck on You, Living in the Jungle, Tikufuna Yesuyo komanso ndaimbanso nyimbo ya Chisoni Nkumatenda mwa njira ina. +Udajambula kuti? Nyimbo zina zidajambulidwa ku Greener Arts Studios msewu wa Chileka ndi Tiya Chalamwendo komanso ku Ralph Records ku Namiyango. Izitu ndi nyimbo za chamba cha reggae momwe onditsata amadziwira. +Mawu kwa Amalawi ndi wotani? Amalawi achilandira chimbalechi ndipo akusangalala nacho. Langa ndi pempho kuti apitirize kutigwira dzanja. Kungoyamikira kokha si kokwanira, akuyeneranso kumatigula zimbalezi. +Tsogolo la fizi silikudziwika Zenizeni pankhani yoti fizi yokwera msukulu za sekondale ndi sukulu za ukachechenjede za boma ipitilire kapena ayi zidziwika posachedwapa unduna wa zamaphunziro ukamanga mfundo, mneneri wa undunawu wauza Tamvani. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Iyi ndi nkhani yomwe Amalawi ambiri akumva nayo litsipa polingalira kuti mwezi wamawawu akuyenera kubowola matumba pankhani ya fizi zomwe posachedwapa unduna wa zamaphunziro udalengeza kuti zakwera. +Malingana ndi mneneri wa undunawu, Rebecca Phwitiko, undunawu ukudikira kalata yochokera ku Nyumba ya Malamulo yokhudza zomwe nyumbayi idamanga pankhaniyi. +Ophunzira a pasekondale ya Zingwangwa mumzinda wa Blantyre. Ena sapitiriza sukulu kaamba ka kukwera kwa fizi Sukulu zonse ndi mtundu wonse Amalawi udziwitsidwa za tsogolo la nkhaniyi posachedwa tikalandira kalata ya ku Nyumba ya Malamulo pa zomwe idamanga, adatero Phwitiko. +Nkhaniyi idakambidwa mNyumbayi pamkhumano womwe wangothawu pomwe aphungu otsutsa boma adadzudzula kukwenza ka fiziku kuti kwabwera panthawi yolakwika. +Ngakhale padali zovuta zingapo, aphunguwo adakambirana nkhaniyo mpaka kugwirizana kuti ndi yofunika kuwunikidwa bwinobwino. +Mneneri wa Nyumbayi Leonard Mengezi adati pakadalipano sangapereke yankho lokhudza zomwe aphunguwo adakambirana poti nkhani ikakambidwa mNyumbayi imayenda mndondomeko zosiyanasiyana isadakhazikitsidwe. +Mmene zidakambidwira mNyumba ya Malamulo muja, nkhaniyi imayenera kupita mmanja mwa komiti ya zamaphunziro kenako komiti yovomereza mfundo za boma isanapite kuunduna ndiye chitsekereni mkhumano mpaka pano sindidamve kalikonse, adatero Mengezi. +Iye adati nkomuvuta kulondoloza nkhaniyi ndi makomitiwo kaamba koti anthu ali patchuthi ndiye sangapereke yankho logwira pokhapokha atabwerera mmaofesi awo tchuthi chikatha. +Nkhawa yaikulu fizi yokwerayi ikaloledwa ndi ana asukulu omwe alibe pogwira kaamba koti akhoza kulephera kuphunzira ngakhale atakhala anzeru. +Koma Phwitiko adati nkhani ya mthumba isabweretse njengunje chifukwa pali ndondomeko zothandizira anthu ovutikitsitsa omwe sangakwanitse kulipira fizi zokwerazi. +Tikudziwa kuti pali anthu ena ovutikitsitsa oti ngakhale fizi zisadakwere ankalephera kulipira, koma pali njira yothandizira anthu oterewa, monga ngongole kwa ophunzira a msukulu za ukachenjede komansothandizo la ulere kwa ophunzira a msukulu za sekondale, adatero Phwitiko. +Iye adati ngakhale zili chonchi, pali ndondomeko yomwe ophunzira amayenera kutsata kuti apeze nawo mwayiwu pofuna kuti okhawo ovutikitsitsa ndiwo azipindula nawo. +Kusankha anthu ovutikitsitsawa kumachitika mmaboma chifukwa ndimo muli anthu omwe amadziwa chilungamo cha anthuwo. Zimafunika mfumu ya kumudzi kwa munthuyo, ofesi ya DC ndi ofesi ya maphunziro (DEM),adatero Phwitiko.Phwitiko adati ophunzira ovutika koma omwe ali ndi abale omwe ali ndi njira zopezera ndalama sadawaike mgulu lopata ngongole kapena thandizo la fizi pofuna kupereka mpata kwa omwe alibiretu podalira. +Iye adati thumba lomwe kumachokera ndalama zothandizirali ndi loperewera kufikira aliyense nchifukwa chake pali kusefaku. +Tidachita dala kupereka ntchito yosefayi mmanja mwa maboma omwe ophunzirawo amakhala chifukwa ndiwo angadziwe wovutika weniweni chifukwa aliyense azifuna kupata nawo ndiye ife sitingadziwe kuti wovutika weniweni ndi uti, adatero Phwitiko.Iye adati kulengeza za tsogolo la fizi zitengera kuti zokambirana zatenga nthawi yaitali bwanji. +Nkhaniyi ili apo, maofesi ambiri kuphatikizapo a mboma ali patchuthi cha Khrisimasi ndi chaka cha tsopano. +Mabungwe omwe si aboma monga la mipingo la Public affairs Committee (PAC) ndi la zamaphunziro la Civil Society Education Coalition (CSEC) adati kukwenza fizi nkofunika kutengera momwe chuma chikuyendera. +Mkulu wa bungwe la CSEC Benedicto Kondowe adati kukwenza fizi ndi njira yokhawo yotukulira maphunziro mdziko muno polingalira kuti zinthu zidakwera ndipo ndi momwe chuma chikuvutira mboma, mpovuta kutiboma palokha lingakwanitse kupereka ndalama zamaphunziro. +Kondowe adati vuto ndi nthawi yomwe boma lakwezera fiziyi polingalira kuti anthu sadakonzekere. +Agwidwa ukapolo ku Ntchisi Madzi achita katondo kwa T/A Malenga mboma la Ntchisi komwe Gulupu Malenga, Peku Wakuda ndi Munkana aletsa anthu a mmudzi mwa Peku Woyera kukhala nawo pa zochitika zilizonse mderali kuphatikizapo maliro, ukwati komanso kupita kumsika wawo waukulu potsatira mkangano wa malo. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Nkhaniyi ikuti mfumu yaingono Peku Woyera idawina mlandu wa malo womwe udaweruzidwa ndi magulupu atatuwa. +Malinga ndi Peku Woyera, magulupuwa ataona kuti zake zayera pamlanduwu, adanenetsa kuti amkhaulitsa. +Akuti asayende: Peku Woyera Chilango chake anthuwa adagwirizana kuti ine ndi anthu a mmudzi mwanga tisiye kukhala nawo pazochitika mpaka kutiletsa kupita kukagula zinthu kumsika wathu waukulu ati kaamba koti ndidawina mlanduwo, idatero mfumuyo, yomwe dzina lake la pamsonkho ndi Tisiyenji Daniyele. +Mfumuyo idati anthuwa adaletsedwanso kukhala nawo pamisonkhano ya chitukuko. +Ngakhale ana awaletsa kutenga nawo mbali pazamasewero, pomwe amayi awathamangitsa kumabanki a mmudzi ndi makalabu a ulimi. Moti ndikulankhula pano mayi wina adamulanda katundu wosiyanasiyana pakhomo yemwe adagula patauni yathu yaingono, Peku Woyera adatero. +Iye adati pano anthuwa akudalira msika waukulu wa Ngombe womwe uli pamtunda wa pafupifupi makilomita asanu. +Peku Woyera adati ngakhale nkhaniyi idatengeredwa kubwalo la milandu komwe adalamulidwa kuti azisonkhana nawo ndi anzawo, magulupuwo akanitsitsa kuchotsa chiletsocho. +Ndife akapolo mmudzi mwathu momwe, adatero Peku Woyera. +Polankhulapo, gulupu Malenga adavomereza za nkhaniyi ndipo adati chidatsitsa dzaye kuti magulupu atatuwo apereke chiletso chokhwimachi ndi mwano womwe Peku Woyera adachita ponyozera zisamani zomwe amalandira. +Malenga adati mwachikhalidwe chawo, zilango monga izi zimaperekedwa kwa anthu amwano ndi cholinga choti aphunzire mwambo. +Iye adati mudzi wonse walandira chilangochi chifukwa udakhudzidwa pamkangano wa malowo. +Ife tikufuna kuti mfumuyi ndi anthu ake azibwera kubwalo akalandira chisamani, koma akapitiriza mwano sitingachitire mwina koma kuwalanga powasala, Malenga adatero. +Koma Clement Zindondo, mmodzi wa akuluakulu a bungwe lomwe si laboma lomwe likutengapo gawo pa achinyamata ndi chitukuko la Ntchisi Organisation for Youth and Development (NOYD), adati anthuwa akusowekera thandizo kaamba koti magulupawa awaphwanyira ufulu wawo wosonkhana ndi anzawo. +Ife tikudabwa kuti bwanji magulupuwa sakulemekeza chigamulo cha bwalo la milandu? Apatu sakusamala za malamulo oyendetsera dziko lino ndipo ndikhulupirira kuti akhoti achitapo kanthu nkaniyi ikawapezanso, Zindondo adatero. +Ana achoke mmindaNduna Mvula yagwa Madera ambiri moti anthu ali kalikiriki mminda kuthira manyowa, kubzala ndi kuwokera koma nkhawa yaikulu yagona pamchitidwe wogwiritsa ana achichepere ntchito za kumunda pofuna kuzemba mtengo wa anthu aganyu. Chaka chino, boma laneneratu kuti silidzasekerera munthu aliyense wopezeka akugwiritsa ana achichepere ntchito mmunda. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi nduna ya zamalimidwe Dr Allan Chiyembekeza pankhaniyi. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu A nduna, tamva mukuchenjeza za mchitidwe wogwiritsa ana achichepere ntchito mmunda, kodi mungatambasulepo bwino pamenepa? Eya, pamenepa tikutanthauza kuti pali anthu ena omwe amaganiza molakwika, mmalo moti azilimbikitsa ana kupita kusukulu, iwo amalemba ana ochepa msinkhu kwambiri ntchito mminda makamaka pano pomwe fodya wagundika. +Mayi ndi mwana wake wachichepere kuchita ganyu mmunda wa fodya. Ana sayenera kugwira ntchito zoposa msinkhu wawo Kodi kumeneku nkulakwa? Kulakwa kwambiri moti ngakhale malamulo a dziko lino zimenezi salola, mwana amayenera kuti azipatsidwa nthawi yokwanira bwino yolimbikira maphunziro. Mwana yemwe amakhalira kugwira ntchito zoposa msinkhu wake monga zakumundazo, amakhala wotopa paliponse ndiye sangalimbikire maphunziro. +Ndimayesa kumeneku nkuphunzitsa mwana ntchito? Ayi kumeneku nkuzunza mwana osati kumuphunzitsa ntchito, ayi. Munthu aliyense amakhala ndi nthawi komanso msinkhu womwe angagwire ntchito zamtundu wina wake osangoti basi tiyeni watopa azikapumira komweko, ayi, nkulakwa kwakukulu kumeneku. +Chiyembekeza: Ana azipita kusukulu, osati kumunda Kodi vuto limeneli ndi lalikulu bwanji? Vutoli ndi lalikulu ndithu komabe poti tidayamba kale kudziwitsa anthu za nkhanza zopita kwa ana makamaka pankhani yowagwiritsa ntchito yoposa msinkhu wawo, anthu ena adamvetsetsa ndipo adasintha koma alipo ena omwe amakhulupirira kuti mwana safuna malipiro ambiri akagwira ntchito ndiye amaona ngati chidule kugwiritsa mwana ntchito kusiyana ndi munthu wamkulu. +Koma zimakhala bwanji anawo sachita kukafunsira ntchitoyo okha? Tikudziwa za nkhani ya umphawi mmene ilili. Ana ambiri akhozadi kukafunsira ntchito okha kuti apezeko mwina chakudya komanso ndalama zodzithandizira kumavuto osiyanasiyana. Ambiri amakhala oti mwina alibe makolo kapenanso iwo ndiwo akuyanganira ana anzawo ndiye palibe chomwe angachite, pogwira alibe. Ambiri mwa ana omwe amakumana ndi nkhanza zamtundu umenewu ali mgulu limeneli. +Nanga munthu utakhala ndi ndalama zolipira aganyu mwana uja nkukupeza kuti akufuna ganyu kuti athandizike ungatani? Apa mpamene pamabwerera mtima wa umunthu. Ngati munthu wamkulu uli ndi udindo wongothandiza mwanayo ngati uli ndi thandizo kapena kumuunikira kuti aike maganizo pasukulu osati maganyu. Ambiri mwa anawa amachokera mmadera momwe ifeyo timakhala ndipo mbiri yawo timayitsata tsono chotiletsa nchiyani kungowathandiza? Nanga poti anthu ena amagwiritsa ntchito ana awo omwe. Anthu oterewa sangadziteteze kuti ndi ufulu wawo poti mwanayo ndi wawo? Malamulo a dziko lino amaneneratu poyera kuti mwana aliyense apite kusukulu osati azikagwira ntchito mmunda, ayi. Palibe munthu yemwe ali ndi mphamvu zilizonse zosintha malamulo amenewa. Ngati lamulo likuti ichi ayi ndi ayi basi. +Ndiye mukungodziwitsa anthu palibe zilango zake? Lamulo lililonse labwino limakhala ndi zilango zomwe olakwa angalandire ataliphwanya. Tikadzapeza munthu wolemba kapena kugwiritsa ana ntchito, tidzamutengera kubwalo la milandu komwe akagamulidwe potsatira zomwe malamulo akunena ndipo sitidzalola kuti anthu oterewa apatside ufulu wosalandira chilango. +Boma lititeteze, atero achitetezo Anthu okhwimitsa chitetezo mmudzi mwa Ntenje, mdera la T/A Machinjiri mboma la Blantyre, apempha boma kuti liwateteze ndi kuwasamala pamene akusaka malo obisala. +Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Iwo ati pantchito yawo monga odzipereka, samalandira kalikonse koma pofuna kuteteza mudzi wawo, kwapezeka kuti nyumba zawo zatenthedwa, katundu waonongedwa. Miyoyo yawo ili pachiswe; iwo ndi mabanja awo akusowa pokhala; ndipo akubisala mtchire. +Police_chimbaula Kumayambiriro a mwezi uno anthu okwiya a mmudziwo adabutsa nyumba zawo, kuwakumbitsa manda komanso kuwamenya powaganizira kuti adapha munthu. +Monga akufotokozera mmodzi mwa achitetezowo, Davie Story, iwo ankateteza Nyadani Dankeni kuti asachitidwe chipongwe ndi anthu okwiyawo amene ankamumenya chifukwa chomuganizira kuti adaba thumba la chimanga. +Iye adati anthuwo adayatsa nyumba zawo ndipo palibe chomwe adapulumutsapo. Adawakumbitsa manda komanso kuwatibula kodetsa nkhawa. Achitetezo onsewo athawamo mmudzimo ndipo akubisala mtchire. +Mkulu wa achitetezowo, Damiano Dindi, adati iye adawathawira ku Nsanje. +Palibe chomwe ndapulumutsa. Chonde, tikupempha boma kuti litithandize chifukwa tazingwa, tilibe pogwira komanso kolowera. Atipezere pokhala komanso atipatse mpamba woti tiyambire moyo wina, adatero Dindi. +Mwambo wa maliro wasintha ku CoM Sukulu ya zaudotolo ya College of Medicine (COM) yasintha momwe mwambo wa maliro panyumba ya chisoni ya pasukuluyo mumzinda wa Blantyre uzichitikira kuyambira pa November 1 2015. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Tsopano, galimoto imodzi yokha ndiyo iziloledwa kufika kumalowa yomwe izikhala ndi anthu osaposera 10. Panja pampanda wa sukuluyu pamene galimoto zimaima, tsopano sipakuloledwanso kuti paime galimoto. +Woyendetsa sukuluyu Margaret Longwe adatsimikizira Msangulutso Lachinayi msabatayi ndipo adati anthu asaope ndi kusinthaku. +Kotenga maliro kuzikhala anthu osaposa 10 Nayo mitengo yosamalira mtembo yasintha. Kuumitsa thupi (embalming) tsopano ndi K50 000 kuchoka pa K10 000, kusunga usiku umodzi ndi K10 000 kuchoka pa K1 000 pamene kusambitsa ndi kuveka ndi K15 000 kuchoka pa K10 000. +China chomwe chasintha nkuti kumaloku sikuzikhalanso mwambo oona nkhope kapena mwambo wa mapemphero ndipo mmalo mwake izi zizikachitika kunyumba kapena kumpingo. +Koma Longwe akuti zonsezi zachitika kufuna kusamala malowa. Palibe chodandaulitsa apa, dziwani kuti iyi ndi sukulu. Kukachitika maliro, kumabwera anthu ambiri mpaka kumachitira mapemphero zomwe si zabwino polingalira kuti apa ndi pasukulu. +Panjapanso pamakhala galimoto zambiri moti ndi mwayi bwezi tikukamba kuti pachitika ngozi koma sizidachitikepo. Ndiye zonsezi tachita kuti tithandizane ndi anthu omwe amagwiritsira malo ano, adatero Longwe. +Iye adati anthu akapita ndi thupi kumaloko, azifunsidwa kaye ngati akwanitse kutsatira malamulo atsopanaowo ndipo akakana, thupilo lizibwezedwa. +Atafunsidwa kuti alankhulepo pa za kukwera mtengo, Longwe adati iyi si nkhani yoti tikambirane. +Sitikulengeza mitengo mnyuzi, ndipo simudamvepo tikulengeza. Aliyense amadzamva komwe kuno akabwera za mitengo. Palibe nkhani pamenepa koma kungowadziwitsa anthu kuti iiyamba ndondomeko zatsopanozi pa 1 November, adatero iye. +Wophwanya lamuliro, akuti adzalipa K50 000. +Nkhawa ikulirakulira pankhani ya zaumoyo Mabungwe omwe si aboma ati mavuto a mgonagona omwe akuoneka pa nkhani za umoyo mdziko muno ndi umboni wakuti chipani cholamula cha Democratic Progressive (DPP) sichikukwaniritsa zomwe chidalonjeza pomwe chinkachita misonkhano yokopa anthu kuti achivotere pachisankho cha chaka chatha. +Kuperewera kwa ogwira ntchito zaumoyo, kusowa kwa mankhwala, kusowa kwa chakudya ndi ganizo la boma lochepetsa chakudya chomwe limapereka kwa odwala mzipatala ndi ena mwa mavuto omwe mabungwewa ati akula padakalipano. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Anamwino kukapereka madandaulo awo ku Nyumba ya Malamulo Mkulu wa bungwe loona za ufulu wa anthu pa nkhani za umoyo, Charles Nyirenda, wati zomwe boma likupanga pochita zinthu modzidzimukira ndi msampha waukulu pa miyoyo ya anthu. +Nyirenda ndi mmodzi mwa oimira mabungwe amene athirapo ndemanga pa zomwe zikuchitika mdziko muno, makamaka pankhani ya za umoyo wa anthu womwe uli pachiswe chifukwa cha mikwingwirima yomwe unduna wa za umoyo akukumana nayo. +Iye adati mmene zinthu zikuyendera pankhani za umoyo, tsogolo lenileni silikuwoneka ndipo kukadakhala bwino boma likadangopanga mfundo imodzi nkuikhazikitsa osati kuvinavina. +Poyamba nkhani imene idavuta ndi yakuti anthu azilipira mzipatala yomwe idatsutsidwa mpaka kuzilala. Pano akuti anthu odwala azidya kamodzi patsiku komanso mankhwala mzipatala sakupezeka. Anthu akumawauza kuti akagule okha, tsono apa zikusiyana pati nkulipira kuchipatala? adatero Nyirenda. +Iye adati chidali chanzeru kuyamba kulipiritsako bola anthu ovutika, koma odwala azidya chakudya chokwanira kuti mankhwala azigwira ntchito mthupi. +Mmodzi mwa omenyera maufulu a anthu mdziko muno, Gift Trapence, adati boma likuyenera kuyankhapo pa nkhawa zomwe anthu, kudzera kumabungwe, akupereka mdziko muno chifukwa lidawalonjeza kukonza mavuto amene akukumana nawowo. +Apa ndi nkhani yoti boma lichitepo kanthu msanga chifukwa lidalonjeza lokha anthu asadalisankhe ndiye zisakhale ngati anthu akupempha ayi koma akungokumbutsa zomwe adalonjezededwa, adatero Trapence. +Mavutowatu akudza patangotha pafupifupi chaka ndi miyezi 6 kuchoka pomwe chipani cha DPP chidayamba kulamula chitapambana pachisankho cha mwezi wa May, 2014. +Chisankho chisadachitike, chipanicho chidalonjeza kuti chidzatukula nkhani zaumoyo poonetsetsa kuti chiwerengero cha anthu ogwira ntchito zaumoyo ndi chokwanira, mankhwala akupezeka mzipatala, kutukula moyo wa anthu ogwira ntchito zachipatala ndi kuchepetsa imfa zokhudza uchembere. +Malonjezowo ali choncho, boma lidaplephera kulemba ntchito madotolo 51 amene adamaliza maphunziro awo kusukulu ya ukachenjede ya College of Medicine, chonsecho ngakhale bungwe la zaumoyo padziko lino la World Health Organisation (WHO) limati madotolo 23 alionse ayenera kuthandiza anthu 10 000, ku Malawi, madotolo awiri amathandiza odwala 100 000. +Ndipo posachedwa, Amalawi zikwizikwi mboma la Rumphi adayenda ulendo wokapereka madandaulo kwa DC wa mbomalo pokhudzidwa kuti odwala akulandira chakudya kamodzi patsiku pomwe akumwa mankhwala ofunika chakudya chokwanira. +Ulendo wokapereka zodandaula za chakudya udakonzedwa ndi mgwirizano wa mabungwe omwe si aboma mbomalo ndipo wapampando wa mgwirizanowo, Eunice Banda, adati zomwe zikuchitikazi zikusonyeza kuti boma likulephera kukwaniritsa lonjezo. +Kutengera zomwe adalonjeza a Pulezidenti kuti sadzalola munthu aliyense kumwalira ndi njala, tikuona kuti zomwe zikuchitikazi zikusonyeza kulephera kukwaniritsa lonjezolo, adatero Banda. +Iye adati si zoona kuti munthu yemwe akulandira mankhwala aziperewera chakudya mthupi mwake chifukwa mankhwala amagwira bwino ntchito ndi chakudya. +Komanso poona kuti sizikuwayendera pantchito yawo, anamwino ena adakaperekanso chikalata chawo ku Nyumba ya Malamulo pozizwa ndi ganizo la boma lakuti anamwino ena amene adalembedwa kale ntchito akayesedwenso. +Mchikalata chawo, anamwinowo adadandaula za momwe ntchito za umoyo zalowera pansi mdziko muno ndi momwe umoyo wa Amalawi wakhudzidwira, zomwe adati gwero lake ndi kusalingalira nkhani za umoyo pakati pa atsogoleri. +Mchikalatachi, adatinso ndi okhudzidwa kuti boma likulephera kulemba madotolo ndi anamwino omwe adamaliza maphunziro awo chonsecho ogwira ntchito zachipatala ndi ochepa, zomwe zimachititsa kuti ntchito yawo iziwawa. +Koma nduna ya zachuma ndi chitukuko, Goodall Gondwe, ati pali mpumulo kumbali nkhani ya chiwerengero cha madotolo ndi anamwino chifukwa maiko omwe amathandiza dziko lino avomereza kuti boma likhoza kugwiritsa ntchito ndalama zina zomwe zidali za ntchito yolimbana ndi malungo, chifuwa chachikulu ndi matenda a Edzi polemba ntchito madotolo ndi anamwino omwe lidalephera kuwalemba. +Chipongwe mmaofesi mwinamu Pali maofesi angapo, maka a boma, omwe amachuluka chipongwe kaya titi mwano polankhula ndi anthu ofuna chithandizo. +Ofesi ngati za Immigration, Road Traffic, komanso mzipatala, kumakhala anthu oti akamakulankhula amachita ngati kuti ndiwe wosazindikira. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ukafika pakauntala, amakufunsa tikuthandizeni? akuyangana kumbali kapena ngati akukuyangana amakuthira diso loderera kapena lotopa nawe. +Anthu ambiri ogwira ntchito mmalowa amakhala ngati adatopa kalekale. Ukapita kufuna chithandizo ukhoza kuyesa ngati mwayambana. Kulankhula ndi munthu wamkulu ngati akuyankhula ndi mwana. +Nthawi zina kuchipatala akakufotokozera ndondomeko ya kamwedwe ka mankhwala ndiye ukapandakumva bwino umachita kulephera kufunsa kuti afotokozenso kuopa kuzaziridwa. +Ukamafotokoza zowawa mthupi, usanamalize nkomwe olemba mwankhwala walemba kale. Amachita ngati ukumutayitsa nthawi. +Kukakhala ku Immigration, chipongwe chimayambira ndi mlonda wa pakhomo. Kulankhula ndi anthu mwachipongwe chokweza ngati ukudzapempha pakhomo pake. +Ukalowa mkatimo ndiye mumakhala chidodo cha dzaoneni. Chiimire pamzere mumangomva za mavuto osatha a network. +Ukafika pamalo oti ujambulitse chithuzi kaya chala, anthu ogwira ntchito ambiri amangoyankhula mwamgwazo, moderera ndi mokalipa. +Mabwana kumaofesi ndatchulawa komanso maofesi ena a boma, mutaunika kagwiridwe ka anthu anu antchito, maka awo amakumana ndi anthu, kuti mutithandize izi zichepe. +Phasipoti kaya laisensi ikatha, umachita kuda nkhawa kuti ukapezekenso mmaofesi amenewa. +Kamatira: Nthenda yosautsa Thenda zina ukazimva mmakutu kuchita kuwawa chifukwa chakuwopsa kwake. Anthu ambiri amataya mtima ndi matenda aja a Edzi komatu kunjaku kulinso matenda ena omvetsa ululu wadzawoneni. Ena mwa matenda otere ndi aja ena amawatcha kamatira. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Socrates Mbewe zokhudza matendawa ndipo machezawo adali motere: Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu A Mbewe, tandifotokozerani kuti mumachokera kuti ndipo mumatani. +Choyamba ine kwathu ndi ku Sawawa kwa mfumu yaikulu Chikowi ku Zomba. Pano ndili muno mu mzinda wa Lilongwe kuthandiza anthu makamaka pankhani ya mankhwala azitsamba. Mwachidule ndine singanga. +Mbewe: Ndachiritsa ambiri odwala kamatira Ndimangomva za matenda a kamatira, kodi amenewa ndi matenda anji? Malume, amenewa ndi matenda osautsa kwabasi. Munthu amangomva mseru, kubaya ndi kupotokola mmimba koma kuti achite chimbudzi kapenanso kutaya madzi amalephera ndiye amakhala akumva ululu koopsa. +Kwenikweni matenda amenewa amayamba bwanji? Pali njira zosiyanasiyana. Zina zachilengedwe zomwe angafotokoze bwino ndi achipatala komanso pali njira za mwa anthu zochita kuponyerana zomwe kuthana nazo kwake ndi kuchikuda basi. +Kuwazindikira kwake akamayamba ungawazindikire bwanji? Ndilankhula kwambiri kumbali yachikudayi chifukwa ndiko ndimadziwa kwambiri monga ndanena kale. Matenda amenewa ali mitundu pawiri. Pali kamatira wamoto yemwe munthu amangomva kutentha mmimba ndi mchikhodzodzo koma kumalephera kudzithandiza ndipo ngati sadathandizidwe, masiku 7 ndi ambiri akhoza kupita. Mtundu wina ndi wa kamatira wozizira yemwe munthu amatha kukhala sabata zitatu akungomva ululu. +Inuyo mudathandizako munthu wa vuto limeneli? Ambirimbiri ndipo amabweranso okha kudzandithokoza chifukwa cha chikumbumtima cha ululu chomwe amakhala nacho. Ndathandiza anthu ambiri mmadera osiyanasiyana osati kuno kokhanso, ayi. +Mankhwala ake mumatani? Pali zizimba zake. Koma chachikulu nchakuti timasema mtengo wa mankhwalawo nkuusakaniza bwinobwino ndiye munthu uja amathira theka la supuni yaingono muphala nkumwa. Akatero amatsegula mmimba kwambiri ndipo zotulukazo zimakhala zakuda kwambiri ngati makala okanyakanya. +Komano oponyerayo amachita bwanji? Pali njira zosiyanasiyana koma machitidwe ake ndi amodzi. Ena amatapa chimbudzi kapena mkodzo olo madindo amatako. Ena amagwiritsa ntchito nsima yotsala kwa munthu yemwe akufuna kulodzayo kapena nkhoko zampoto momwe mudaphikidwa nsimayo. Machitidwe ake, amatenga zomwe ndatchulazi nkusakaniza ndi mankhwala kenako nkuika muchithu chosachucha kapena kudontha. Ambiri amakonda bango ndipo mkatimo amasakanizamo singano kuwonjezera ululu uja. +Ndiye kuchira kwake ndi kwa asinganga basi? palibenso njira ina ngati zili zoponyeredwa, apo bii ndiye kuti wolodzayo akhululuke nkumumasula mnzakeyo. Zikakhala zachilengedwe ndiye mapilitsi aliko kuchipatala, munthu amatha kumwa nkutsekula mmimba bwinobwino. Koma chachikulu choti mudziwe nchakuti si onse omwe amadziwa mankhwala ake, ena sadziwa koma amangokakamira chifukwa chofuna makobidi. Singanga weniweni akaunika, ngati zili zachilengedwe amamuuza chilungamo munthu. +Koma muzonse zomwe mwakumana nazo inuyo mumapeza kuti chimachititsa anthu kuponyerana nthenda yoopsayi nchiyani? Nkani yaikulu imakhala dumbo. Ngati munthu wina amachita nawe nsanje ndiye akuganiza njira yokuzunzira kapena ngati anthu adayambana ndiye winayo akufuna kumvetsa mnzakeyo kuwawa mpamene izi zimachitika. +Chaka ndi miyezi inayi ali mchipatala osaimirira Maloto a Alineti Molosi wa zaka 15 odzakhala namwino akhoza kufera mmazira ngati madotolo sakwanitsa kumuchiza nthenda yozizira miyendo yomwe idayamba msuweni wake atamubaya ndi mpeni. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Alineti akuti ululu omwe akusauka nawo panowu gwelo lake ndi chipatso cha ndimu chomwe amafuna kuthyolera mwana wa azakhali ake mumtengo omwe uli pakhomo pomwe msuweni wakeyo amakhala. +Iye adati ili lidali khumbo chabe chifukwa sadathyole chipatsocho ataona kuti pakhomopo padalibe munthu aliyense ndipo adabwerera kuti eni khomo akafika apite kukapempha koma mwatsoka msuweni wakeyo adamuona ndipo adamutsatira. +Alineti (wagona) pakama kuchipatala ndi mayi ake Adafikira kundinena kuti ndaba mandimu ndipo ine ndikukana adatenga mpeni nkundibaya pakhosi kumbuyo ndipo kuchoka apo ndidadzazindikira ndili mchipatala koma sindikumbuka momwe ndidabwerera, adatero Alineti. +Padakalipano, msungwanayu watha chaka ndi miyezi 4 osayima kapena kukhala tsonga mchipatala cha Kamuzu Central kaamba kakuti thupi lake lidazizira kuchokera mchiuno mpaka kumapazi. +Mai ake a Alineti, Leniya Molosi adati izi zidachitika mwezi wa August, 2014 mmudzi mwa Nthanje T/A Malengachanzi ku Nkhotakota pomwe mwana wakeyo adakachita tchuthi kwa azakhali akewo. +Iwo adati msungwanayu adali mu sitandade 7 ndipo amachita bwino mkalasi moti samakayikira kuti akadakwanitsa maloto odzakhala namwino. +Ntchito ya unamwino amayifunadi chifukwa kuyambira kale ukamufunsa chomwe akufuna kudzakhala mtsogolo amanena za unamwino moti apa chisoni chikundipweteka kwambiri chifukwa mchipatalamu akumaona anamwino tsiku ndi tsiku, adatero Leniya. +Chomvetsa chisoni kwambiri nchakuti makolo ake a msungwanayu ali pa vuto la zachuma moti pocheza ndi Msangulutso sadabise kuti chilowereni mchipatalamo, palibe mbale yemwe adabwerako kudzawazonda kaamba kosowa mayendedwe. +Maiyu adandandaula kuti kuti kwa chaka ndi miyezi 4 tsopano sadaone amuna ake ndi ana ake ena 6 omwe adawasiya ku Nkhotakota ndipo sakudziwa kuti adzawonana nawo liti. +Msangulutso adalephera kulankhula ndi dotolo yemwe akuthandiza msungwanayu koma mayi akewo adati vuto lomwe dotoloyo adapeza ndi lakuti mpeniwo udakalasa mtsempha waukulu zomwe zidapangitsa kuti ziwalo zina zizizire. +Tikungokhala muno sitikudziwa kuti tidzatuluka liti poti vuto lake likuoneka kuti ndi lalikulu. Nkhawa ina ndi ana anga omwe ali kunyumba ndi kumunda chifukwa ndimo timapezera chakudya ndi ndalama, adatero Leniya. +Ndimafuna mwamuna wadzitho Felix Mwamaso ndi mmodzi mwa akatswiri osewera nkhonya mdziko muno. Koma kuti zonse zizimuyendera tayale choncho pali nthiti yake, Queen, yemwe amamuchengeta. Koma nanga awiriwa adakumana bwanji? Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndinkafuna mwamuna wadzitho, nthawi zonse ndinali kudikirira kuti ndidzapeze wamaonekendwewa. Nditamuona Felix akuponya maso pa ine panthawi ya nkhonya yake ku Obrigado Leasure Park mumzinda wa Mzuzu, ndinati mwayi suposa apa, adatero Queen polongosola mmene adakumanirana koyamba ndi mwamuna wake. +Adayanjana magazi: Queen ndi Felix Mwamaso Kuchokera panthawi imene adaonana pamalo ankhonyawa mu August chaka cha 2013, awiriwa adagwa mchikondi chozama ndipo kenako adamanga banja chaka chomwecho mwezi wa November. +Malinga ndi maongokedwe ake, Queen adandipatsa chikoka choti ndimutengere panyumba. Mwamwayi nditaponya mawu oti ndamukonda sadavute, ndipo ndidazitenga kuti ndi zomwe amayembekezera, adatero Felix. +Awiriwa akukhalira limodzi ku tauni ya Chibavi ku Mzuzu. +Lachitatu sabata yatha, chisangalalo chokumbukira kuti akwanitsa zaka zitatu ali limodzi ngati banja chidali cha mtima bii ndipo chidachitikira pamalo ena achisangalalo ku Mzuzu otchedwa Sports Cafe. +Asimbe lokoma ndani?: Civo, Manoma aswana mu Standard Bank Pali ntchito mawa pabwalo la Civo mumzinda wa Lilongwe pamene timu ya Civo United ichapane ndi Mighty Be Forward Wanderers mndime yotsiriza ya chikho cha Standard Bank. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Matimu onse adapatsidwa sabata imodzi yoti akonzekere masewerowa ndipo mawali ndi lomwe amene wotenga chikhochi adziwike. Silver Strikers ndiyo idatenga chikhochi chaka chatha itapuntha Azam Tigers 2-0. +Civo yafika mndimeyi kawiri, mu 2009 pamene idakanganthidwa ndi Tigers kudzera mmapenote komanso mu 2010 pamene idakhaulitsidwa ndi Moyale kudzeranso mmapenote. +Manager wa Civo, Rashid Ntelera wati palibe chatsopano chomwe timu yawo yakonzera osewera ngati angatenge chikhochi mawa. +Malamulo athu ali momwe alili. Kupambana masewerowa ndiye kuti tili ndi K10 miliyoni, osewera adzagawana K6 miliyoni yomwe ndi ndalama yambiri, osewera akudziwa kale zoyenera kuchita komanso ubwino wotenga chikhochi, adatero iye. +Wanderers yatengapo chikhochi kawiri, mu 2012 pamene idaumbudza Silver 2-0. Idachiteteza mu 2013 pokhaulitsanso Silver 1-0. +Manager wa Wanderers Steve Madeira akuti chilichonse chakonzeka kuti mawali alange Civo ndi kutenga chikhochi kachitatu. +Mukudziwanso kuti Wanderers ikamamenya mchikho imaikirapo mtima kwambiri. Komanso anyamata akudziwa kuti kungatenga K10 miliyoni ndiye kuti akatamukiratu. Tikudziwa kuti masewerowa akakhala ovuta komabe osapotera nyerere adziwe kuti tikachita zakupsa, adatero. +Momwe matimuwa ayendera kuti afike mndimeyi. +Wanderers ndiyo yasewera masewero ambiri chifukwa idachita kuvoteredwa ndiye idayambira mndime ya chipulula pamene idatulutsa Mafco 4-3 kudzera mmapenote. +Mndime ya makotafainolo, Civo idachapa Dedza Young Soccer 2-0 pamene Wanderers idathowa Red Lions 1-0. +Mndime ya semifainolo, Civo idalanga Bullets 2-1 pamene Wanderers idatuwitsa Blue Eagles 1-0. Lero matimu amene akhala akulanga anzawo mchikhochi akuyenera kulangana. +Ndi Walter, Mijiga Kapena Yabwanya? Atatsatsa mfundo zawo masiku apitawa, omwe akulimbirana maudindo kubungwe loyendetsa masewero a mpira wa miyendo la Football Association of Malawi (FAM) akhala akukumana maso ndi maso pazisankho zomwe zikuchitika lero. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Nthumwi zokwana 36 zochokera kunthambi za FAM ndi zomwe zitaponye voti pamsonkhano waukulu womwe ukuchitikira mboma la Mangochi. +Akuimanso: Nyamilandu Omwe akupikisana paudindo wa pulezidenti ndi yemwe pakalipano ali pampandowu, Walter Nyamilandu, Wilkins Mijiga komanso a Willy Yabwanya Phiri. +Akuluakuluwa sabata yathayi adali kalikiriki kupereka mfundo zawo pazomwe akufuna adzachite akasankhidwa paudindowu. +Polankhula mumzinda wa Lilongwe, Nyamilandu adalonjeza kuti akapambananso adzakhazikitsa ndondomeko zoonesetsa kuti mpira wa mmakwalala ukupita patsogolo komanso kuti mpira ukubweretsa ndalama zochuluka maka mmakalabu osiyanasiyana. +Wakonzeka: Mijiga Kumbali yake Yabwanya adalonjeza kuti adzasula aphunzitsi a mpira ambiri omwe azitha kuphunzitsa anyamata achisodzera ndi cholinga choti luso lawo lipite patsogolo. +Naye Mijiga pomema anthu kuti amusankhe, adati adzakhazikitsa njira zopezera ndalama ndi cholinga choti osewera, oyimbira komanso oyendetsa mpira azilandira ndalama zambiri. +Pakalipano zikuonetsa kuti Nyamilandu atha kutenganso mpandowu kaamba koti mwa nthambi zisanu ndi zinayi za bungwe la FAM, zisanu ndi ziwiri zidalengezetsa kuti zili pambuyo pake. +Ali momo: Yabwanya Phiri: Nthambi imodzi yokha ya Super League of Malawi ndi yomwe ikuti ili pambuyo pa Mijiga pomwe ya National Referees Committee ndi yomwe ikuti ili pambuyo pa Yabwanya. Koma zioneka komweko chifukwa voti ikhala yachinsinsi. +Omwe akupikisana pampando wa wachiwiri kwa pulezidenti ndi Tiya Somba-Banda ndi James Mwenda. Mpikisano pampando wa wachiwiri kwa wachiwiri kwa pulezidenti uli pakati pa Pikao Ngalamila ndi Othaniel Hara. +Ku Nkhoma sakugona ndi mthirira Amati mmera mpoyamba. Ukalephera kukonzekera koyambirira ntchito yonse imayenda mwapendapenda mpaka zipatso zake zimakhala zokhumudwitsa. Ino ndi nyengo ya dzinja ndipo ulimi wagundika ndi wamvula, koma alimi ochangamuka pano ayamba kale kukonzekera za mthirira wachilimwe chomwe chikubwera kutsogoloku. Ena mwa alimi omwe akuonetsa chitsanzo chabwino pakukonzekera mthirira wamtsogolo ndi a ku Nkhoma mboma la Lilongwe. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi wapampando wa gulu la alimiwa, Lingilirani Chikhwaya pazomwe akuchita, motere: Chikhwaya: Sitivutika kumbali ya chakudya Ndikudziweni wawa Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ine ndine Lingilirani Chikhwaya ndipo ndine wapampando wa alimi a mthirira omwe amathandizidwa ndi bungwe la Vision Fund Malawi kudzera mthumba la ngongole za ulimi la Mthirira Loans. +Mulipo alimi angati? Tonse tilipo alimi 222 omwe timathandizidwa ndi Vision Fund Malawi koma aliyense ali ndi munda wakewake momwe amalima mbewu yomwe iye akuona kuti imuchitira bwino ndipo apindula nayo. +Ndi mbewu zanji zomwe zimalimidwa kwambiri? Ambiri amalima chimanga, nyemba, tomato, anyezi ndi ndiwo zamasamba zosiyanasiyana. Ambiri mwa ife timakonda kasakaniza monga kubzala chimanga limodzi ndi nyemba kapena kugawa kuti mbali ina tomato, ina anyezi ndipo ina masamba monga chomoliya, mpiru kapena kabichi. +Ulimi umenewu ukukupindulirani bwanji? Ulimiwu tikupindula nawo kwambiri chifukwa usadabwere, ambirife tinkavutika kwambiri kupeza zipangizo zaulimi dzinja likafika kusowa pogwira, koma pano zinthu zidasintha. Tikamachita mthirira wathu timakhala tikusunga pangonopangono ndalama mwinanso nkumaguliratu zipangizo zaulimi nkumasunga. Tikatero, dzinja ngati lino likafika timakhala tilibe nkhawa. Kupatula apo, sitivutika kumbali ya chakudya chifukwa timati tikamadya zamvula, zamthirira zikucha kuti zamvulazo zikamadzatha, tidzayambe kudya zamthirira. +Mukuoneka kuti muli kalikiriki mmunda wa mthirira pomwe lino ndi dzinja simukupotoza pamenepa? Ayi ndithu, umu ndimo timachitira. Kuteroku tayambiratu kukonzekera mthirira wachilimwe chikubwerachi. Pali zambiri zomwe timayenera kupangiratu monga kusunga madzi okwanira, kuteteza maiwe anthu kuti asadzadze komanso kutchingira mmalo momwe mumathamanga madzi kuti asaononge nthaka. Kungolekerera nthaka imakokoloka ndiye poti munthu udzayambe kulima ulimi wamthirira zofuna zimachuluka monga kusonkhanitsa manyowa obwezeretsera nthaka yomwe idakokolokayo. +Panopa yakula ndi ntchito iti? Monga ndanena kale, pakalipano ntchito yaikulu ndi yosunga madzi. Ulimi wathu wamthirira timadalira msinje ndiye chaka ndi chaka ngati panopa timatchingira kuti madzi asathawe. Timapanganso mizere ikuluikulu yotchinga madzi kuti azilowa pansi kuti mvula ikadzatha, pansi padzakhale chinyezi kwathawi yaitali tisadayambe kuthirira. +Tafotokozankoni nkhani ya misika, mumagulitsa kuti zokolola zanu? Ambiri mwa ife timadalira kugulitsa kumisika ndi kupikulitsa kwa anthu omwe amakagulitsa kumsika. Si misika yodalirika, ayi, komabe timapezamo kangachepe. Pakalipano omwe amatithandiza ndi ndalama za ngongole a Vision Fund Malawi akutithandiza kuyangana misika yodalirika moti posachedwapa tikhala tikusimba lokoma. +Mudalingalirako zopanga magulu ogulitsira katundu wanu pamodzi? Maganizo amenewo ndiwo tikupanga tsopano nchifukwa chake tili kalikiriki kusakasaka misika yokhazikika komanso paja ndati pakalipano mlimi aliyense ali ndi ufulu wolima mbewu yakukhosi kwake ndiye tikufuna kuti tikapeza msika wokhazikika, tizidziwa mbewu zoyenera kulima. Nanga si msika wapezeka kale? Kaya tsogolo la ulimi wanu mukuliona bwanji? Tsogolo ndi lowala kwabasi chifukwa momwe tidayambira ndi pomwe tili pano zikusiyana kwambiri. Mbewu zomwe tinkakolola kale ndi zomwe timakolola pano zimasiyana kwambiri chifukwa pano tidapatsidwa upangiri wapamwamba ndi alangizi odziwa ntchito yawo. Chiyembekezo chathu nchakuti mzaka zikudzazi tizidzalima ndi kukolola mbeu zoti mwinanso nkumadyetsa chiwerengero cha anthu ochuluka chifukwa, mwachitsanzo, chaka chino tathandiza anthu ambiri ndi chimanga chomwe tidalima kusikimu ndipo nafenso tapeza phindu lochuluka kwambiri. +Malangizo anu ndi otani kwa alimi anzanu? Malangizo anga ndi oti alimi asamakonde kukhala pansi ayi. Ntchito yathuyi imasiyana kwambiri ndi ntchito zina chifukwa ife ndiye timadyetsa mtundu wonse. Tizionetsetsa kuti mvula ikamapita kumapeto, ntchito ya kusikimu yayamba ndipo chilimwe chikamapita kumapeto, tizionetsetsa kuti tayambiratu kukonzekera ulimi wa mthirira wotsatirawo ngati momwe tikuchitira ifemu. Izi tikuchita apazi ndi chiyambi chabwino chifukwa sitidzakhala ndi ntchito yambiri mthirira ukamadzayamba. +Nthula: Abambo ofooka kuchipinda achangamuke Akuti abambo ena amafooka pamene akucheza ndi akazi awo chifukwa cha zina zomwe zimasowekera pamene machezawa ali mkati. Ichi nchifukwa chake makolo akale amakhulupirira kuti pakhale nthula kapena kuti mthunduwere zomwe zimachangamutsa amuna oterewa. Ibra Monjeza wa mmudzi mwa Sauka kwa T/A Malemia mboma la Zomba ndiye akufotokoza izi kwa BOBBY KABANGO. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Monjeza kufotokozera anthu za kufunikira kwa nthunduwere Tidziwane bwinobwino. +Ine ndi Monjeza, ndine mlimi komanso anthu amandidziwa bwino ndi ulangizi wanga. Ulangizi wokhudza mabanja komanso ulimi. +Ndi ulangizi wanji omwe mutipatse lero? Ndikupatsani ulangizo omwe ndimawafotokozera anthu pafupifupi tsiku lililonse. Uwu ndi ulangizi kwa amayi zomwe ayenera kuchita kuti bambo asamafooke pamene akucheza nawo. +Ndiye amayenera atani? Nkhani ndi nthula basi. Kugwiritsa ntchito nthula molondola ndiye kuti zako zayera, bambo abwekera nthawi zonse ndipo sangafooke. +Nthula nchiyani? Ndi zibalobalo za kamtengo kakangono kamene kamakhala ndi minga. Ena amati nthunduwere ndipo mbuzi zimadyanso. +Mwati zimathandiza chiyani? Dziwani kuti macheza pakati pa bambo ndi mayi amakhalabwino ngati aliyense akusangalala. Bambo amakhala nthawi yaitali pamene akucheza ndi mayi ngati mayiyo wapanga zomusangalatsa. Apa ndi pamene tikuti nthula zimagwira ntchito kuti machezawa akhale a nthawi. +Nthula ndiye zimapanga chiyani? Zimakometsera machezawo. Kuti athe nthawi pakufunika nthula kuti nonse awiri akhutitsidwe. +Mumazitani nthulazo kuti zifike pamenepa? Umafunika uthyole nthulayo koma usankhe yoti ikupita koola, imakhala yoti ili biii! kuda. Dziwani kuti amayi ndiwo amagwiritsira ntchito nthulayi osati amuna. Imangopangitsa kuti mwamuna asangalale pamene akucheza. +Ndiye munthu wa mayiyo atani akatenga nthulayo? Amayingamba pakati ndi kumagwiritsira ntchito. Pakutha pa sabata mayiyo amakhala wasinthiratu, akati acheze ndi mwamuna zimakhala zabwino chifukwa mwamuna amasangalala ndithu. +Amazigwiritsa bwanji ntchito ndipo chimathekacho nchiyani? Akangoyicheka pakati nthulayo, basi apite kwa mayi aliyense amene ndi wamkulu mdera lawo ndipo akamuuza bwino momwe angaigwiritsire ntchitomo. Akaigwiritsa ntchito bwino, amakhala mkazi woti mwamuna amasangalala naye pamene akuchita macheza ndipo ngakhale amuna ofooka amalimbikitsidwa. +Tafotokozani bwino. +Sindinena. Dziwani kuti kale mtundu ulionse umadziwika ndi zochita zake. Angoni, Achewa ndi ena timawadziwa momwe akuchitira kuchipinda koma masiku ano aliyense amatsata njira zomwe akufuna kuti asangalatse amuna ake. Kale Alhomwe timawadziwa ndi mikanda, koma lero upezanso ena omwe ndi Alhomwe alibe mikanda. Izitu zikusonyeza kuti chikhalidwe chidasokonekera ndipo aliyense akupanga chomwe akufuna. Izi ndikunenazi ndi zachikhalidwe ndiye sindinganene wamba. +Osati mukungotinamiza apa? Kodi inu mudakwatira? Kapena mudayambapo mwacheza ndi mayi ndipo mudasiyanitsapo? Chifukwa ngati mudachitapo izi, bwezi mutandimvetsa. Sindikunama, izi ndi zoona. +Inuyo mudasiyanitsapo? [Akuseka.] ndikudziwa chomwe ndikunena. +Pewani chipalamba posamala mitengo Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kampani yogula fodya ya Limbe Leaf Tobacco Company yati makolo azitsogolera ana pantchito yobzala mitengo kuti mdziko muno musadzakhale chipalamba chomwe chingabweretse mavuto adzaoneni. +Mkulu wa bungweli Rodney Haggar adanena izi Loweruka pomwe kampaniyi inkapereka mbande za mitengo pasukulu ya pulayimale ya Mwakhundi kwa T/A Khongoni mboma la Lilongwe. +Haggar adati kutsogoza achinyamata pantchito zobwezeretsa chilengedwe kungathandize kuti achinyamata azikula ndi mtima wozindikira kufunika kosamala chilengedwe kuti mtsogolo muno mavuto a kusintha kwa nyengo adzachepe. +Iye adati vuto lalikulu ndi loti anthu ambiri amakanika kusamala mitengo yobzalabzala uku ali yakaliyakali kudula mitengo yachilengedwe, zomwe zimachititsa kuti mabweredwe a mvula asinthe komanso kunjaku kuzitentha mopitirira muyeso. +Achinyamata azikula ndi mtima wosamala chilengedwe Mitengo mwalandirayi muisamale kuti ikule komanso musalekere pomwepa, ayi. Pezani mitengo yambiri ndipo paliponse pomwe palibe mitengo mubzalepo mitengo. Tayesetsaninso kutsogolera achinyamata pantchito yobzala mitengo kuti akamakula azikhala ndi malingaliro obwezeretsa chilengedwe, adatero Haggar. +Mkuluyu adati mitengo ndi yofunika pantchito zosiyanasiyana makamaka nkhani zaulimi ndipo kulekerera pantchito yobzala mitengo nkuweta chipalamba chomwe zotsatira zake zingadzaike Malawi pamoto. +Mkulu wa bungwe la mgwirizano wa mabungwe a zaulimi Tamani Nkhono-Mvula adagwirizana ndi maganizo olimbikitsa achinyamata kukula ndi mtima wosamala chilengedwe. +Nkhani yaikulu apa ndi kumanga maziko oti mtsogolo muno zinthu zisadzavute. Chilichonse panopa pankhani ya ulimi chikudalira mitengo. Kuti mvula igwe molongosoka ndi mitengo; nthaka ndi iyi mukuyiona nokha ikungokokolokayi chifukwa chosowa chitetezo; kutentha ndiye nkosayamba, adatero Nkhono-Mvula. +Dzinja lililonse kumakhala nthawi yobzala mitengo koma mvula ikatha mitengo yambiri imafota nkuuma chifukwa chosowa chisamaliro. +Chikondi chiphetsa amuna awiri Nthawi zina chikondi chikafikapo, chimazunguza mutu. Amuna awiri mmaboma a Machinga ndi Zomba adzikhweza sabata yathayi nkhani ya chikondi itavuta. +Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Mneneri wapolisi kuchigawo chakummawa Thomeck Nyaude watsimikizira Msangulutso za imfa ya Chrispine Botomani wa zaka 22 wa mmudzi mwa Silulu kwa T/A Nkula mboma la Zomba ndi Moses Ndege wa mmudzi mwa Tchuka kwa T/A Chikwewu mboma la Machinga. +Nyaude adati woyamba kudzipha adali Botomani amene adadzipha pa 25 October pamene adadzimangirira kunkhalango ya Chilunga mumzindawo. +Iye adati Botomani ankasalidwa ndi apongozi ake akazi pomunena kuti ndi mphawi ngakhale iye ndi mkazi wake akhala zaka zisanu ndi kudalitsidwa ndi mwana mmodzi. +Mu 2013, mwamunayo adapita ku Lilongwe kukayangana maganyu. Apa makolo ake a mkaziyo adamuthawitsa mwana wawo kuti azikakhala ku Mangochi kwa achibale. +Koma chifukwa chomukonda mwamuna wake, mkaziyo adadziwitsa Botomani za ulendowo ndipo mwamunayo adapita ku Mangochiko komwe adagwirizana kuti asinthe malo okhala, adatero Nyaude. +Mneneri wa polisiyo wati awiriwa adasamukira kwa Chikanda mboma la Zomba komwe amakhala pamene makolo ake a mtsikanayu amakhala ku Matawale mbomali. +Koma wapadzala adavumbulutsa wa patsindwi pamene mkaziyo adauza mwamuna wake kuti amuperekeze kwa makolo ake koma ati adamuuzitsa mwamunayu kuti sakafika pakhomopo chifukwa amaonerana mkodi ndi apongoziwo. +Akumuperekeza, adakumana ndi apongoziwo. Adayamba kumutukwana motheratu zomwe zidakwihyitsa bamboyo, adatero Nyaude. +Apa, iye adathamangira kunkhalangoko komwe adakadzikhweza koma ati adasiya kalata ya masamba anayi koma mbali imodzi ya kalatayo idati: Apongozi mutsale bwino, mundisamalire mkazi wangayo padziko lapansi pano koma kumwamba tikakumana [ndipo] tikakwatirananso. Mundilelere mwana wanga.chikondi si chuma koma kugwirizana. +Koma Nyaude wati palibe amene wamangidwa ndi imfa ya bamboyu ponena kuti palibe mlandu womwe wapalamulidwa. +Mawu okha si mlandu. Inuyo kutukwanizana ndi mnzanu palibe mlandu ulionse. Ndiye palibe amene akuyenera kuzengedwa mlandu chifukwa cha imfa ya Botomani, adatero Nyaude. +Pa nkhani ya ku Machinga, Nyaude adati malemu Ndege adakwatira akazi awiri omwe samasangalala kuti mwamunayo azipita kwa mkazi wina. +Amayiwa amakhala nyumba zosiyana, ndiye mkazi aliyense adamupatsa masiku ake amene amakhala ndi bamboyo zomwe sizimasangalatsa akaziwa chifukwa aliyense amafuna mwamunayu akhale wake, adatero. +Iye wati izi zidasokoneza bamboyu amene adaganiza zodzipha podzimangirira mkazi wake wamkulu ali kumunda pa 1 November 2015. +Anatchezera Anatchereza Ndikumanyozedwa Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Anatchereza, Zikomo chifukwa cha malangizo amene mukumapereka. Ine ndili pabanja ndipo pano tikutha miyezi 7 ndipo timakondana kwambiri. Koma panopa ndikunyozedwa ndi mkazi yemwe mwamuna wangayu adamukwatira poyamba ineyo kulibe. Kodi pamenepa nditani? Edna, Blantyre Zikomo mayi Edna, Choyamba ndikumbutseni kuti chikondi ndi anthu awiri, wachitatu ndi kapasule. Ndikhulupirira mudayamba mwamvapo mawu amenewa. Ndiye apa mwanena nokha kuti inu ndi amuna anu mumakondana kwambiri, ine ndingoti umo ndiye ziyenera kukhalira chifukwa maziko a banja langwiro ndi chikondi, chikondi chake chozama. Pamene pali chikondi palibe mantha, koma dziwani kuti nthawi zonse padzakhala ena ena ansanje omwe sakondwera anthu akamakhala mwachikondi mbanja. Nkutheka kuti mkazi wakale wa mwamuna wanu akuchita nsanje ndi inu malinga ndi mmene mukukhalira mbanja mwanu nchifukwa chake akuyesayesa kuti akusokonezeni. Ndi kavuwevuwe ameneyo, musamamulabadire. Sindidziwa kuti mkazi mukunenayo banja ndi mwamuma wanu lidatha bwanji, ndiye nkhani yoti mukumanyozedwa ndi mkaziyo muwauze amuna anu. Ngati sakuchitapo china chilichose chokuthandizani, muli ndi ufulu kuitengera nkhaniyi kubwalo la milandu kuti chilungamo chioneke chifukwa pokunyozani akukuphwanyirani ufulu wanu. +Ndidalirebe? Agogo, Ndine mnyamata wa zaka 23 ndipo ndimagwira ntchito ku Mangochi. Asananditumize kuno ndidakumana ndi mtsikana wina wake dzina lake Zione B, wa zaka 20 ndipo panthawi imene ndinkamufunsira iyeyu adali ndi chiphaso choyendera kunja (passport). Mu June mnzake wina adamuuza kuti wamupezera ntchito ku Joni koma panthawiyo adamuyankha kuti sangapite nkundisiya ine pandekha. Mu August achimwene ake adandiitana kunyumba kwawo ku Lilongwe kukakambirana zokhudza ukwati wathu choncho tidagwirizana za mwezi wa December kuti tidzapange chinkhoswe. Chokhumudwitsa nchakuti mkaziyu adapita ku Joni pa 7 November ndipo adandiimbira foni kamodzi kokha mmene adangofika kumeneko ndipo mpaka pano sakuimbanso. Ndikamuimbira panambalayo sikupezekanso. Mmene zililimu kumbali ya chikondi chathu zikuta- nthauzanji?Ndidalirebe kapena ayi? Mmin, Mangochi Zikomo F. Mmin, Mosafuna kuchulutsa gaga mdiwa, wachikondi wakoyo alibe chikondi ndi iwe ndipo ndakaika ngatidi adapita ku Joniko kukagwira ntchito ndipo ndikuganiza kuti kudali kuphiphiritsa chabe mmene amati mnzake wamupezera ntchito. Mmene ndikuonera ine ali kubanja ameneyo! Nchifukwa chake adangoimba foni kamodzi kukuuza kuti wafika ku Jonjiko ndipo kenaka adasintha nambala kuti olo uimbe musamalankhulanenso. Ndiye langizo langa ndi loti usataye naye nthawi ameneyo, wapita basi. Yangana wina amene angakupatse chikondi chenicheni, osati wachiphamaso. Atsikana ambiri makono ano chilungamo chikumachepa, kaya nchifukwa chiyani? Nchifukwa chake maukwati a masiku sakulimba chifukwa chosowa chilungamo. Ambiri akumakhala ndi zibwenzi zoposa ziwiri zamseri, aliyense nkumamulonjeza kuti akwatirana naye. Zokhumudwitsa kwabasi. +Akundikaniza Ndine mayi wa zaka 30, ndili pabanja ndipo ndili ndi ana 5. Ndimalakalaka nditabwerera kusukulu koma abambo akunyumba amakana. Ndipange bwanji? Nzomvetsa chisoni kuti abambo akukukanizani kubwerera kusukulu. Ndi amayi ochepa kwambiri omwe amaganiza ngati inu, kuika maphunziro patsogolo. Ndikhulupirira bamboo aliyense akhoza kukhala ndi chidwi ndiponso wonyadira kuti mkazi wake akulimbikira sukulu chifukwa maphunziro ndiye chitukukocho. Ndakunyadirani kwambiri. Koma mwina pali zifukwa zake zimene amuna anu akukukanizirani kuti mubwerere kusukulu, mwina nkutheka kuti ana ena ndi aangonoangono moti adzasowa chisamaliro chanu mukapita kusukulu. Poti simunalongosole bwinobwino kuti sukulu yake ndi yotani mpovuta kuti ndikuthanzizeni kwenikweni, koma ngati zonse zili bwinobwino mbanja lanu, pitirizani kukambirana za ubwino wa sukulu pofuna kutukula banja lanu. Ndaonapo ine amayi akuluakulu apantchito, monga aphunzitsi, akupita kusukulu pofuna kuonjera maphunziro. Akakhoza amatha kukwezedwa pantchito ndipo potero amathandiza amuna awo pankhani ya chuma mbanja. Sukulu sinamatu paja. Mwina chilipo chimene akukukayikirani amuna anuwo kuti mukabwerera kusukulu sizikhala bwino. Ndikhulupirira si choncho. OFUNA MABANJA Ndikufuna mkazi woti ndimange naye banja, wa zaka 18-25, akhale wapantchito. Amene angasangalatsidwe aimbe pa 0882 234 843. Zachibwana ayi, ndili siliyasi. +Ndine wa zaka 32.Ndikufuna mwamuna wa zaka 35-45. Wofuna aimbe pa 0881 042 774. +Ndine mnyamata wa zaka 25 ndikufuna mkazi wa zaka 18 mpaka 26 wofuna banja. Aimbe pa 0995 154 501 Sindili pantchito koma ndikufuna mkazi wa zaka 25-35. Wosangalatsidwa aimbe pa 0992 395 279. +Ine ndi wa zaka 32 ndikufuna mwamuna wabanja koma akhale wa siliyasi. Akhale wa zaka za pakati pa 35 ndi 40, woopa Mulungu. Tandiimbirani pa 0888 437 123. +Nanawa: Mlowammalo wa kupitakufa Matenda a HIV/Edzi asokoneza miyambo ina monga mwambo wa kupitakufa, womwe umapereka mphamvu kwa fisi kuti akakonze maliro pocheza ndi namfedwa kwa sabata ziwiri ndipo machezawo amachitika katatu patsiku. Chifukwa cha matendawa, kwabwera njira ya nanawa yomwe yazilalitsa mwambo wa kupitakufawu. BOBBY KABANGO adali mboma la Nsanje komwe adacheza ndi mlembi wa nyakwawa Masanzo kwa T/A Mlolo. +Chisale watuluka nkumangidwanso Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Kodi amfumu tawapeza? Ayi, iwowa adzukirira kudimba. Akuyembekezereka kubwerako madzulo chifukwa ntchito yakula kumeneko. +Tidalire kuti inu mutithandiza pa vuto lathu? Musakaikenso, ndine mlembi wa amfumuwo ndiye palibe chomwe sindikuchidziwa chokhudza mudzi uno ndi miyambo yomwe timatsata. +Mkaka: Mwambo wa nanawa timangomwa mankhwala othamangitsa imfa Kodi mwambo wa kupitakufa ukuchitikabe kuno? Zikuchitika koma mobisa chifukwa momwe matenda a Edzi aopseramu sungayerekeze kumachitabe mwambowu. Amabungwe akhala akufika kumemeza anthu kuti miyambo yoipa, monga umenewu, itheretu ndipo zipatso zake zikuonekadi pano. +Ndiye mukutani kuti imfa ithawe pakhomo? Timagwiritsa mankhwala a nanawa amene amathamangitsa imfa pakhomo. Kuno anthu ambiri tikutsata zimenezi. +Nanawa nchiyani? Ndi mankhwala amene singanga amachita pakhomo pamene pagwa maliro. Anthu, maka achibale, amamwa mankhwalawo molandirana ndipo pakhomopo pamakhala bwino. +Zimachitika nthawi yanji? Maliro akachitika monga lero, mawa timakaika ndiye timasweretsa tsiku limodzi pamene timasonkhana kudzasesa. Nthawi yosesa mpamene mwambo wa nanawa umachitika. Mungathe kuchita mwambowu nthawi iliyonse kaya ndi masana kapena madzulo. +Kodi mankhwalawa mumatemera kapena mumadya? Mankhwalawa ali pawiri. Ena amakhala a madzi. Amawaika mkapu ndiye aliyense wachibale amalandirana mankhwalawo kumamwa pangono mpaka nonse achibale akukwaneni. Pamene mankhwala ena amawaika kudenga kwa nyumba yomwe mumagona malemuwo. Mumawasomeka kudenga mbali yomwe kuli khomo kuti anthu akamalowa mnyumbamo azigwira mankhwalawo. +Mukutanthauza wachibale aliyense amayenera amwe mankhwalawo? Zimatero kumene. Nonse mumalandirana, kumwa pangono basi, aliyense kamodzi komanso momapatsirana. +Nanga achibale amene sadafike pamwambowo mumawatani? Achibale amene nthawi ya malirowo kapena tsiku la kusesalo palibepo, timawasungira mankhwalawo. Mankhwala ake ndi amene tawasomeka kudenga aja. Tsiku lomwe akonza zodzafika pakhomopo, timawalandira ndi kuwatengera kunyumba yomwe kudachitika malirowo. Ndiye pamene tikulowa mnyumbayo, timawapatsa mankhwala aja kuti agwire. Akangotero basi amabwezeretsa mankhwalawo kudengako. +Amachitanso china chiti? Palibe, ngati agwira mankhwalawo ndiye kuti nawonso akonzedwa ku imfa yomwe idakangogwa pakhomopo. +Nthawi yomwe munkatsata mwambo wa kupitakufa zinkakhala bwanji? Maliro akachitika chonchi, timapeza fisi kuti apite kunyumba yomwe kwachitika malirowo akacheze ndi namfedwayo. Katatu patsiku kapena zikavuta atha kumacheza nawo kawiri patsiku kwa sabata ziwiri. Fisiyu ntchito yake idali yoti achotse mzimu wa imfa womwe wakuta pakhomopo. +Mpaka katatu? Ndiye zidalikolikotu Hahaha! Eeh, amasangalala kwambiri koma pano zimenezi zidatha. +Nanga akamwalira wamkazi, afisi aakazinso amapezeka? Ayi, zikatere ndiye tinkapanga mankhwalawa kapena apo ayi mupemphe banja lina kuti likupitireni kufako. +Mpira uthera panjira wosewera atamwalira Anthu akugwedeza mitu yopanda nyanga ku Choma, mboma la Mzimba kaamba ka imfa ya mnyamata wa Fomu 3 pasukulu ya sekondale ya Choma yemwe adaombana ndi goloboyi poti agwire mpira ali paliwiro lamtondo wadooka lokagoletsa Lachisanu lapitalo. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Patsikulo, timu yomwe Isaac Phiri wa zaka 20 amasewera imapimana mphamvu ndi timu yachisodzera ya pa sukulupo. +Isaac amasewera ngati wogoletsa. +Malinga ndi mphunzitsi wamkulu pasukulupa, Mathews Phiri, yemwenso amaonerera masewerowa, izi zidachitika patangodutsa mphindi 30 mpira utayamba ndipo udathera pomwepo. +Phiri adati Isaac yemwe adali wogoletsa wodalilika, adanyamuka ndi mpira mwa liwiro zedi ndi cholinga chokagoletsa, ndipo atayandikira golo kuti aponyere muukonde naye goli adachoka pagolo ndi kuombana ndi mnyamatayo. +Iye adati, apa onse adagwa pansi ndipo Isaac adayamba kudzigwiragwira moonetsa kuti ali muululu woopsa. +Malinga ndi lipoti la chipatala, kuombana pachifuwa kwa awiriwo kudachititsa avulazane mkati komanso womwalirayo apweteke kapamba. +Tidathamangira konko, pamodzi ndi achipatala omwe adalinso pompo, tidayesa kumutsira madzi koma sizidathandize ndipo apa mpamene tidathamangira naye kuchipatala chomwe chilli pafupi ndi bwalo lamaseweroli komwe atamupima adatiuza kuti watisiya, Phiri adatero. +Iye adati masewerawo, omwe amakonzekera masewero akulu ndi timu ya sukulu ya pulaiveti ya Chiume adathera pomwepo ndipo aliyense sakumvetsa zomwe zidachitikazo. +Koma Levi Mwale yemwe ndi dokotala wa timu ya dziko lino adati ngozi zotere sizichitikachitika. +Mwale adati nthawi zambiri zikachitika zimakhala kuti wosewera mpira wameza lilime lomwe limatseka modutsa mpweya. +Iye adati vuto ndi loti masewera ambiri mdziko muno, amaseweredwa opanda akatswiri a za udotolo. +Anthu sadziwa kuti munthu akavulala akusewera mpira, amasamalidwa bwanji, Mwale adatero. +Iye adati ndi zachisoni kuti imfa zoterozi zimagwa chifukwa chosowa chidziwitso. +Tikufunika tiphunzitsidwe kasamalidwe ka ovulala mu mpira, kuyambira matimu a supa ligi, maligi aangono komanso a mmadera ndi msukulu, Mwale adatero. +Polankhulapo mneneri wa apolisi mchigawo cha kumpoto Maurice Chapola adati Issac yemwe amachokera mmudzi mwa Msafiri T/A Mtwalo mbomalo adamwalira kaamba kovulalira mkati. Iye adati adavumbulutsa izi ndi a chipatala cha Mzuzu. +Chapola adatsimikiza kuti Isaac adakomoka ataombana ndi goli ndipo achipatala cha Choma ndiwo adalengeza za imfa yake ndi kutumiza thupi lake ku chipatala cha Mzuzu kukafufuza chidadzetsa imfayi. +Anatchezera Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndimukhulupirirebe? Agogo, Ndili pachibwenzi ndi mtsikana wina wake ndipo ndakhala naye mwezi umodzi. Vuto ndi loti iye ali ndi mimba ya miyezi iwiri. Kwathu sakudziwa. Ndiye nditani, agogo? Malizani, Blantyre A Malizani, Funso lako ndi lovuta kukuyankha chifukwa sukufotokoza bwinobwino chomwe chidachitika kuti bwenzi lako wakhala nalo mwezi umodzi koma akupezeka kuti ali ndi pathupi pamiyezi iwiri. Ndiye ukuti utani pamenepa? Ndikuyankha pokufunsa kaye mafunso awa: Kodi iwe ndi dokotala kuti udziwe kuti mimba ya bwenzi lakolo ndi yamiyezi iwiri? Kodi udadziwa bwanji kuti ali ndi pathupi? Adachita kukuuza ndi iyeyo kapena udachita kumva kwa ena? Nanga pathupipo ndi pa yani? Kodi iweyo, Malizani, udayamba wakhala malo amodzi ndi mtsikanayo? Ndafunsa dala mafunso amenwa chifukwa mayankho ukuwadziwa ndiwe. Ngati zili zoona kuti chibwenzi chanu chatha mwezi umodzi koma mtsikanayo akupekeza kuti ndi wodwala kale, miyezi iwiri, monga ukunenera, ndiye kuti adachimwitsana ndi wina wake, osati iwe. Tsono zili ndi iwe kuvomereza kuti mimba ili apo, ngakhale si yako, umukondabe ndipo mwana akadzabadwa udzamulera ndi kumusamalira. Koma nkutheka? Iwe ndinu Yosefe kuti uvomereze kuti udzatero popanda vuto lililonse? Ganiza mofatsa ndipo chilungamo choti uchite chioneka chokha. Inde, nkutheka kuti bwenzi lakolo ndi lachilungamo ndipo lidakuuza za pathupipo. Ndi ochepa amene angatero. Ndiye zili ndi iwe kupitiriza chibwenzi chanu kapena kuchithetsa mwamtendere. +Ndazama mchikondi Agogo, Ndimadziwa kuti kukhala pachibwenzi uli pasukulu ndi zolakwika, koma nanga ine nditani? Ine ndine mtsikana wa zaka 16 ndipo ndili mchikondi ndi mnyamata wina yemwe timakondana kwambiri ndipo timathandizana nkhani za sukulu, za kutchalitchi ndi zina zotero ndipo tinalonjezana kuti sitidzagonana mpaka titakwatirana. Koma vuto ndi loti kwathu amandikaniza kupanga chibwenzi ati zimalakwitsa sukulu ndipo utha kutenga mimba. Ndimayesetsa kuti ndithetse chibwenzichi koma ndimakanika chifukwa ndimamukonda kwambiri, ndiye nditani ine? Amene akukuuza zoti kukhala ndi chibwenzi uli pasukulu sakulakwa, mwanawe. Uwamvere! Poyamba zimayamba choncho, malonjezo, kuthandizana, izi ndi izi, kenaka mutu umaima ndipo pamene uzidzati hii! ndapanga chiyani? zako zitada. +Ndithu, mwana iwe, nthawi yokhala ndi chibwenzi siinakwane chifukwa udakali wamngono ndipo uli iwe apo ndi pamsinkhu wovuta zedi. Samala, ungadzanongoneze bondo. Zinazi ndi bwino kuzipewa. +Panopo ukuona ngati mnzakoyo akukukonda mchoona pamene ali ndi kampeni kumphasa. Amayamba kukulowa pangonopangono ngati thekenya kenaka udzangozindikira zinthu zalakwika, wakuchimwitsa! Limbikira sukulu kaye, zachibwenzi pambuyo. Sukulu ndi zibwenzi siziyenderana. +Imva izi, mwana iwe, mawu a akulu amakoma akagonera. +Ofuna Mabanja Ndikufuna mkazi wa zaka pakati pa 18 ndi 21. Ndine mphunzitsi. Amene angasangalatsidwe aimbe pa 0881 939 676. Zachibwana ayi, koma zasiliyasi. +Ndine mwamuna wa zaka 27 ndipo ndikufuna mkazi wokongola woti ndimkwatire. Mkaziyo akhale wosachepera zaka pakati pa 21 ndi 24, woti adalemba kale mayeso ake a MSCE komanso wopanda mwana. Ngati ali pantchito zitha kukhalanso bwino kwambiri. Omwe angandifune andiyimbire pa 0884 322 798. +Ndine mtsikana wa zaka 19 ndipo ndikufuna mwamuna womanga naye banja. Akhale wa zaka zosapitirira 27. Wotsimikiza aimbe pa 0885 552 045. +Ndili ndi zaka 28 ndipo ndili ndi ana awiri. Ndikufuna mwamuna woti ndimange naye banja koma akhale woti adayezetsapo magazi ndipo adapezeka ndi kachilombo ka HIV. Wasiliyasi aimbe pa 0881496 409. +Ngozi zanyanya chaka chinoApolisi Apolisi ati ngozi za pamsewu mdziko muno zachuluka ndi 18 pa ngozi 100 zilizonse poyerekeza ndi chaka chatha nyengo ngati yomweyi. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mkulu wa apolisi mchigawo cha pakati, George Kainja, ndiye adanena izi Lachinayi potsegulira msonkhano wa komiti yoyanganira za chitetezo cha mmudzi kulikulu la polisi mchigawo chapakati. +Iye adati chomvetsa chisoni nchakuti ngozi zambiri zimakhudza ana asukulu ndi akabaza ndipo zimachitika kwambiri chifukwa chosatsatira malamulo a pamsewu ndi kuyendetsa galimoto zosayenera kuyenda pamsewu. +Kainja: Apolisi ena akuipitsa mbiri ya polisi Taluza miyoyo yambiri chifukwa cha ngozi za pamsewu koma kufufuza, zambiri mwa ngozizi zimachitika chifukwa chophwanya malamulo a pamsewu ndi kugwiritsa ntchito galimoto zosayenera kuyenda pamsewu, adatero Kainja. +Iye adati nthawi zina galimoto zosayenera kuyenda pamsewu zimapezeka pamsewu kaamba ka ziphuphu zomwe apolisi apamsewu amalandira kwa oyendetsa ndi eni ake magalimoto kuti asawagwire. +Kainja adadzudzula mchitidwe wa ziphuphu za pamsewu kuti zimabwezeretsa chitukuko cha dziko mmbuyo komanso zimaononga mbiri ya polisi. +Anthu podzudzula amangoti apolisi, osasiyanitsa kuti apolisi ake ati. Posachedwapa kwatuluka malipoti angapo omwe akusonyeza kuti mpolisi mukuchitika zachinyengo kwambiri ndipo ili si bodza, adatero Kainja. +Mkuluyu adapempha komiti yoyanganira ntchito zachitetezo cha mmudzi kuti azilimbikitsa ntchitozi kuti chitetezo chizipita patsogolo chifukwa apolisi alipo ochepa kuyerekeza ndi momwe zimafunikira. +Iye adati chigawo cha pakati chokha chili ndi apolisi 451 omwe amayembekezeka kuteteza anthu oposa 7 miliyoni kutanthauza kuti wapolisi mmodzi amateteza anthu 1 600 mmalo mwa anthu 500 pamalamulo a mgwirizano wa maiko. +Iye adatinso mchitidwe wozunza maalubino udakula mchakachi kaamba ka mphekesera zakuti mafupa a anthuwa ndi amtengo wapatali ndipo adati iyi ndi ntchito ya anthu kudzera mmagulu a chitetezo cha mmudzi kuteteza anthuwa. +Kalikiliki popewa ngozi za madzi Pamene nkhani yolosera mvula ili mkamwamkamwa, boma lati lili pakalikiliki kuti madzi osefukira amene amasautsa mmadera ena chaka chino lisakhale vuto la mnanu. +Ambiri mwa anthu omwe amakhudzidwa ndi omwe amakhala mmphepete mwa madzi makamaka mmaboma a kuchigwa cha Shire: Chikwawa ndi Nsanje. Chaka chatha kusefukira kwa madzi kudankitsa ndipo kudakhudza maboma 18 mdziko muno, mpaka mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adati dziko lino ndi la ngozi, zimene zidachititsa kuti mabungwe ndi maiko athandizepo. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Malinga ndi mkulu wa nthambi yoona ngozi za dzidzidzi Bernard Sande, chomvetsa chisoni nchakuti ngozi zotere zikachitika boma limaononga ndalama za nkhaninkhani kusamala anthu okhudzidwawo ndi kubwezeretsa zinthu zoonongeka. +Chaka chino chokha boma lidati likufunika K215 biliyoni zoti likonzetsere zinthu zomwe zidaonongeka ndi madzi osefukira dzinja lathali pomwe anthu, ziweto ndi katundu wawo zidakokoloka. +Zambiri mwa zofunika kukonzedwazo ndi milatho, masukulu, misewu, zipatala ndi zogwiritsa ntchito mmalowa zomwe zidaonongeka. +Sande adati chomvetsa chisoni nchakuti anthu omwe amakhudzidwa kawirikawiri amakakamira kukhala kumadzi komwe sikuchedwa kusefukira ndipo adati chaka chino boma likufuna anthu onse okhala mmalo oterewa achokeretu mvula isadayambe. +Tayamba kale kulangiza anthu kuti achoke mmadera momwe mumasefukira madzi ndipo tionetsetsa kuti onse achoka chifukwa sitikufuna kuti chaka cha mawa tizidzakambanso nkhani yomweyi, adatero Sande. +Iye adati anthuwa amati sangachoke mmalomo chifukwa makolo awo adamwalira ndi kuikidwa momwemo komanso malo olima ndi kuweterapo ziweto zawo ali momwemo. +Malinga ndi T/A Maseya ya mboma la Chikwawa, anthu amavuta pankhani yamalo chifukwa amakhulupirira kuti kusiya malo omwe padagona mizimu ya makolo awo kuli ngati kuwagalukira nchifukwa chake safuna kusamuka. +Iye adati vuto lina ndi lakuti malo omwe anthuwo amakhala ndi aakulu kutanthauza kuti atati asuntha ndiye kuti komwe angapiteko malo sangakawakwanire potengera pokhala ndi polima pomwe. +Kupatula kukhulupirira kukhala pamodzi ndi mizimu ya makolo awo, vuto lina ndi malo okhalapo ndi kulima kumtundako, adatero Maseya. +Paramount Kyungu ya ku Karonga adagwirizana ndi Sande pankhaniyo ndipo adati palibe phindu kutaya moyo chifukwa chokakamira manda ndi minda mmalo mosuntha kupita kumtunda ndi kudzabwerera mchilimwe. +Zionetsero ponseponse Nyimbo imene idavuta pa Wenela tsiku limenelo idali ya Lucius Banda, Jennifer. +Mundiuzire Jennifer Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ayeayeyeye Mundiuzire afatse Ayeayeyeye Kokafuna maunitsi akatengako Edzi. +Abale anzanga ndiye kudali kuvina ngati tili ku Crossroads Hotel kuyembekezera kudzaonera ukwati woyera pa 20 December pano. +Atabwera Abiti Patuma, adati akudzangonditsanzika chifukwa unali ulendo wautali amati auyambewo. +Pa Wenela pandilaka. Lero lino ndikupita ku Chitipa, kumene kuli Amalawi enieni a mtima monga Chilembwe. Pamene wapondedwa si bwino kunena kuti akulu mungathe kuchotsako phanzi lanu chifukwa langa lalowa pansi pa phanzi lanulo, adatero Abiti Patuma. +Palibe chimene ndidatolapo. +Kumenekotu anthu sakuyesa, akwiya chifukwa kuchipatala akupereka chakudya kamodzi patsiku ngati kundende. Tsono munthu angachire bwanji pamene sakudya? Sakukambatu za kusowa kwa mankhwala, adatero Abiti Patuma. +Abale anzanga, ndikamati Abiti Patuma amandisokoneza ndimanena chifukwa cha zinthu ngati izi. +Adandiyanganitsitsa. +Nchifukwa chake Billy Wayaya akamapita yekha pamsewu kusonyeza mkwiyo palibe amamumvetsa. Umbuli ndi nthenda yoopsa zedi. Pajanso kuli za anamwino kuyenda pamsewu. Za ana asukulu otsekeredwa chifukwa cha zionetsero ndiye sitinganene, adapitiriza. +Apa ndipo ndidayamba kuzitolera. Paja zionetsero ndiye zangoti mbweee! Zisandikhudze. Zidzandikhudza mukadzakonza chionetsero chonena kuti mukufuna Adona Hilida abwerera kuno ku Wenela. Oipa athawa yekha ndi amodzi mwa mawu omwe adandisiyira atate anga, ndidatero. +Za Adona Hilida usachite kukamba. Iwotu ali ngati asirikali akuluakulu a ku Germany amene adazunza Ayuda zaka zapitazo. Nkhondoyo itangotha, asirikaliwo adali kuthawa mdzikolo, ena kukagwidwa ku Brazil mpaka, adatero Abiti Patuma. +Ukutanthauza kuti akusiyana ndi Nelson Mandela yemwe adayamba kukhala moyo wothathawa kunja asanakhale paulemerero? Inetu sindikudabwa, chifukwa amabwera ndi zinthu zodabwitsa. Pajatu ndiwo adationetsa kuti nzotheka otsutsa kubera chisankho! Adationetsanso kuti kusolola mwakathithi nkotheka ngakhale wina aomberedwepo, ndidatero. +Mmaso mwanga ndimaona mayi wina pompano pa Wenela amene ankakonda kupachika litaka la nsalu paphewa, ati mudzi wonse udziwa palibe ali ndi zitenje zochuluka kuposa iye pano pa Wenela. +Abale anzanga dziko laipa ili, kunjaku kwaopsa zedi. +Zoona Moya Pete alemba ntchito munthu wosamudziwa polingalira kuti palibenso amadziwa ntchito kuposa iye? Akuluwa phindu lawo ndimalephera kulimvetsa. Pajatu masiku ano kuti upeze ntchito yapamwamba uyenera kudziwana ndi akuluakulu. Palibe cha mahala, adatero Gervazzio ngati wadzuka kutulo. +Koma imene amayambitsayo akadaikwanitsa? Ndiye ndangomva kuti ayamba akana kumulemba ntchitoyo? Koma apa pakuonekanso kuti pavuta. Kapena pakufunika kachionetsero kapadera? adabwekera Abiti Patuma. +Kupitakufa? Mbiri yakale imeneyo! Matenda a HIV/Edzi asokoneza miyambo ina monga mwambo wa kupitakufa, womwe umapereka mphamvu kwa fisi kuti akakonze maliro pocheza ndi namfedwa kwa sabata ziwiri ndipo machezawo amachitika katatu patsiku. Chifukwa cha matendawa, kwabwera njira ya nanawa yomwe yazilalitsa mwambo wa kupitakufawu. BOBBY KABANGO adali mboma la Nsanje komwe adacheza ndi mlembi wa nyakwawa Masanzo kwa T/A Mlolo. +Mkaka: Mwambo wa nanawa timangomwa mankhwala othamangitsa imfa Tidziwane, achimwene Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ndine Joseph Mkaka. +Kodi amfumu tawapeza? Ayi, iwowa adzukirira kudimba. Akuyembekezereka kubwerako madzulo chifukwa ntchito yakula kumeneko. +Tidalire kuti inu mutithandiza pa vuto lathu? Musakaikenso, ndine mlembi wa amfumuwo ndiye palibe chomwe sindikuchidziwa chokhudza mudzi uno ndi miyambo yomwe timatsata. +Kodi mwambo wa kupitakufa ukuchitikabe kuno? Zikuchitika koma mobisa chifukwa momwe matenda a Edzi aopseramu sungayerekeze kumachitabe mwambowu. Amabungwe akhala akufika kumemeza anthu kuti miyambo yoipa, monga umenewu, itheretu ndipo zipatso zake zikuonekadi pano. +Ndiye mukutani kuti imfa ithawe pakhomo? Timagwiritsa mankhwala a nanawa amene amathamangitsa imfa pakhomo. Kuno anthu ambiri tikutsata zimenezi. +Nanawa nchiyani? Ndi mankhwala amene singanga amachita pakhomo pamene pagwa maliro. Anthu, maka achibale, amamwa mankhwalawo molandirana ndipo pakhomopo pamakhala bwino. +Zimachitika nthawi yanji? Maliro akachitika monga lero, mawa timakaika ndiye timasweretsa tsiku limodzi pamene timasonkhana kudzasesa. Nthawi yosesa mpamene mwambo wa nanawa umachitika. Mungathe kuchita mwambowu nthawi iliyonse kaya ndi masana kapena madzulo. +Kodi mankhwalawa mumatemera kapena mumadya? Mankhwalawa ali pawiri. Ena amakhala a madzi. Amawaika mkapu ndiye aliyense wachibale amalandirana mankhwalawo kumamwa pangono mpaka nonse achibale akukwaneni. Pamene mankhwala ena amawaika kudenga kwa nyumba yomwe mumagona malemuwo. Mumawasomeka kudenga mbali yomwe kuli khomo kuti anthu akamalowa mnyumbamo azigwira mankhwalawo. +Mukutanthauza wachibale aliyense amayenera amwe mankhwalawo? Zimatero kumene. Nonse mumalandirana, kumwa pangono basi, aliyense kamodzi komanso momapatsirana. +Nanga achibale amene sadafike pamwambowo mumawatani? Achibale amene nthawi ya malirowo kapena tsiku la kusesalo palibepo, timawasungira mankhwalawo. Mankhwala ake ndi amene tawasomeka kudenga aja. Tsiku lomwe akonza zodzafika pakhomopo, timawalandira ndi kuwatengera kunyumba yomwe kudachitika malirowo. Ndiye pamene tikulowa mnyumbayo, timawapatsa mankhwala aja kuti agwire. Akangotero basi amabwezeretsa mankhwalawo kudengako. +Amachitanso china chiti? Palibe, ngati agwira mankhwalawo ndiye kuti nawonso akonzedwa ku imfa yomwe idakangogwa pakhomopo. +Nthawi yomwe munkatsata mwambo wa kupitakufa zinkakhala bwanji? Maliro akachitika chonchi, timapeza fisi kuti apite kunyumba yomwe kwachitika malirowo akacheze ndi namfedwayo. Katatu patsiku kapena zikavuta atha kumacheza nawo kawiri patsiku kwa sabata ziwiri. Fisiyu ntchito yake idali yoti achotse mzimu wa imfa womwe wakuta pakhomopo. +Mpaka katatu? Ndiye zidalikolikotu Hahaha! Eeh, amasangalala kwambiri koma pano zimenezi zidatha. +Zitukuko pa Wenela Nyengo yasintha abale anzanga. Chikuchitika nchiyani? Pano pa Wenela, usiku winawo kudatentha zedi moti usiku onse ndimangokhalira kudzikanda. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kutembenuka ndiye kudali kosayamba, thukuta lili kamukamu! Koma kungocha, mphepo idali kuomba moopsa, mosasula madenga. Ndipo tsiku linalo kudazizira ngati wafikanso mwezi wa June! Chikuchitika nchiyani? Lero kumva kuti kwina mphepo ya mkuntho yasasula madenga, kenako kumvanso kuti kwina mphenzi yapha anthu. Chavuta nchiyani. +Tidakhala pa Wenela tsiku limenelo kudikira Moya Pete ankati adzatsegulire chitukuko china. Tonse tidakonzeka, kuitanitsa gologolo, amayi a chisamba aja lero asintha makaka kuchoka ku Polisi Palibe kupita ku Dizilo Petulo Palibe. Eyatu, zaka 51 za kuvina! Gogo ujatu adatipeza tikuvina ndiye mungaletse ndani kuvinira Moya Pete? Iye walakwanji kuti tisamuvinire? Adafika Moya Pete ndi mdipiti wa galimoto zochuluka. Adabwera ndi anzake ambiri, pajatu ali ndi abwenzi ochuluka. +Adati tilowoloke njanji, nkumalowera kanjira kachidule kopita ku Mbayani. Tikuyenda chomwecho, tidapeza liboni lomwe amaika kusonyeza kuti pakutsegulidwa chitukuko. +Ndayamika kwambiri, abale anzanga, lero lino tikutsegulira msewu umenewu kwambiri. Gogo uja palibe chimene adapanga pano pa Wenela kwambiri, adatero Moya Pete. +Abale anzanga, kodi nkhani zotsegula mipita imeneyi nkuchita kutulutsa munthu wamkulu kuchoka kunyumba yachifumu ija adamanga gogo uja. +Ndikuuzeni kwambiri. Male Chauvinist Pigs siyidzatiuza zochita pano pa Wenela. Mbamba ndikunenetsa kwambiri. Ndipo posachedwapa, ndikatsegulira gawo la msewu wa ku Amwenye ku Limbe, adaonjezera chomwecho. +Abale anzanga, sindikudziwa za inu koma ndisaname, zimandivuta kumvetsetsa zinthuzi. Zili ngati Adona Hilida kunena kuti akulephera kubwerera pano pa Wenela chifukwa palibe wawapatsa nyumba. Kodi zaka zonse ankagawa abakha ankagona mumtengo? Nchifukwa chake nanenso ndidavomereza mawu a Moya Pete kuti momwe zinthu zikukhalira pano pa Wenela, ndithu ana obwera mtsogolo adzatitemberera. +Pano pa Wenela pakufunika anthu a maganizo ngati Che Guevera, Nelson Mandela ngakhalenso Fidel Castro. Kupanda apo, tipitiriza kuchemerera otsogolera kusolola akatchula dzina la Mama Tuge, adatero Abiti Patuma titafika malo aja timakonda pa Wenela. +Vuto la madzi lakula ku Mulanje Anthu a mdera la mfumu Mpweshe komanso Khunyeliwa mdera la T/A Juma mboma la Mulanje akuvutika kuti apeze madzi aukhondo chifukwa cha kuchepa kwa mijigo mmidzi mwawo. +Mudzi wa Mpweshe, womwe uli pamtunda wa pafupifupi makilomita 55 kuchokera pa boma, uli ndi mjigo umodzi okha pomwe mabanja oposa 400 amakatunga madzi. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Malinga ndi mfumu Mpweshe, kuchepa kwa mijigoko kukudzetsa mavuto osiyanasiyana chifukwa amayi ndi atsikana amakhala pamizere italiitali kuti apeze mpata wotunga madzi, komanso ambiri mwa iwo amayenda ulendo wautali kuti akafike komwe kuli mjigowo. +Mjigo womwe uli mmudzi mwathuwo adaukumbira kumbali kwenikweni kwa mudzi wathu komwe ndi kumalire ndi mudzi wa Khunyeliwa womwenso uli ndi mavuto a madzi, choncho kutunga madzi pamjigowo kumakhala kolimbirana kaamba ka kuchuluka kwa anthu, idatero mfumuyo. +Malinga ndi mmodzi mwa ogwira ntchito muofesi yoona za madzi mboma la Mulanje, Medson Bwezani, ndondomeko za madzi zimati mjigo umodzi umayenera kupereka madzi kwa anthu okwana 200, pomwe mpope umodzi umayenera kumagwiritsidwa ntchito ndi anthu 250. +Mjigo wina womwe mudziwo udali nawo utaonongeka mchaka cha 2007 mudziwo sudalandirenso mjigo wina. +Mfumu Mpweshe idauza Mana kuti kwa zaka pafupifupi 8 mudziwo wakhala mmavuto otere ngakhale kuti iwo ndi anthu a mmudzi mwawo akhala akunena za vutolo kukhonsolo komanso kwa mabungwe omwe akugwira ntchito mderalo kuti awathandize. +Poyankhulapo, mkulu woyendetsa zitukuko mboma la Mulanje, Humphrey Gondwe, adati izi nzomvetsa chisoni chifukwa kupereka madzi aukhondo kwa anthu ndi imodzi mwa ngodya za chitukuko cha dziko lino. +Gondwe adati vuto lomwe lilipo ndi lakuti pazitukuko zomwe atsogoleri a mderalo adapereka chaka chino kukhonsolo kuti iwathandize, sadaikepo chitukuko cha madzi. Choncho nkovuta kuti khonsolo iwapatse mjigo anthuwo msanga. +Chinthu china chomwe chikukulitsa vuto la madzilo nchakuti mmudzimo mulibe chitsime kapenanso mtsinje woti anthu angamakatungeko madzi ogwiritsa ntchito zina. +Alosera mvula kugwa mochuluka Nthambi yoona za nyengo ya Department of Climate Change and Meteorological Services (DCCMS) yati mvula yamphamvu ikhala ikugwa kwa masiku angapo motsatizana. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Uwu ungakhale mpumulo polingalira momwe mbewu zafotera mminda komanso lingakhale tsoka polingalira ngati mvulayo ingachulukitse monga zidalili chaka chatha mmadera ena. +Mchikalata chosonyeza momwe nyengo ikhalire masiku angapo akudzawa, nthambiyo idati mvula yamphamvuyi ikhala ikugwa dziko lonse pafupifupi sabata yatuthu kuyambira lachinayi lapitali. +Kaamba ka ngamba, chimanga china chidanyala Mphepo yomwe ikuomba kuchokera mmadera osiyanasiyana, ipangitsa kuti mvula yamphamvu kwambiri izigwa makamaka kuyambira Lamulungu pa 17 January, 2016. Mmadera ambiri, anthu ayembekezere nyengo yotentha masana panthawiyi, idatero nthambiyi mchikalatacho. +Mkulu wa nthambiyo Jolam Nkhokwe adati mmasiku angapo apitawa, mvula adayeserako mmadera a mchigawo chapakati ndi kumpoto pomwe mmadera a kumwera, mvulayi imagwa monyentchera. +Mneneri wa nthambiyo, Ellen Kululanga, adati izi nzosadabwitsa chifukwa ndimo zimakhalira kukakhala mphepo ya El Nino monga momwe azanyengowa adalengezera kumayambiriro a mvula. +Malawi ali mmphepete mwa zigawo ziwiri za Africa kumwera ndi kummawa zomwe zimapangitsa kuti kabweredwe ka mvula kazisiyana. Mvula imavutirako mchigawo cha kumwera kaamba kakuti chili mbali ya kumwera kwa Africa. +Chigawo cha kumpoto chomwe chili kumbali ya kumawa kwa Africa, mvula imachulukirapo moti ndi mphepo imeneyi ya El Nino, madera a kumwera mvula ivutirapo pomwe kumpoto ndi madera ena pakati zinthu zikhalako bwino, adatero Kululanga. +Ogwira ntchito zotukula ulimi mmaboma osiyanasiyana adatsimikizira nyuzipepala ya The Nation kuti ngamba yomwe idagwayi yaononga mbewu zambiri mmadera osiyanasiyana. +Ena mwa omwe adatsimikizira izi ndi wachiwiri kwa oyendetsa ntchito za Blantyre ADD Aggrey Kamanga komanso otukula ntchito zaulimi mboma la Machinga Palichi Munyenyembe omwe adati mvula idadula ndipo alimi ali ndi nkhawa. +Pac ifuna mayankho pa za kukwera kwa mitengo Kukwera kwa zinthu mdziko muno kwaika Amalawi pamoto wa mavuto zomwe zachititsa kuti bungwe la Public Affairs Committee (PAC) likonze msonkhano wopeza mayankho a mavutowa. +Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Mkulu wa bungweli Robert Phiri watsimikizira Tamvani za msonkhanowu koma wati tsiku ndi malo amsonkhanowu adziwitsidwa posakhalitsapa. +Kukweza kwa mitengo ya madzi ndi K45 pa K100 iliyonse, mitengo ya magetsi ndi K39 pa K100, shuga ndi K10 pa K100 iliyonse komanso zina zakudya ndi kukwera kwa chiongola dzanja choperekedwa munthu akakongola ndalama kubanki ndi zinthu zomwe zapangitsa kuti moyo ukhale wopweteka. +Msonkhano wa PAC mu 2012 kudali chitetezo chokhwima zedi Izi ndi zomwe si zidakhazike chete bungwe la PAC pamene akonza nkhumano kusaka mayankho. +Bungwe la PAC likudziwa nyengo zowawitsa zomwe Amalawi akudutsamo. Chomwe tikufuna nchakuti Amalawi tikhale pamodzi kuti tipeze mayankho pa mavutowa, adatero Phiri. +Titamufunsa ngati msonkhanowo ungabale zipatso, Phiri adati iwo akukhulupirira kuti ukhala ndi chophula kusiyana nkuti aliyense azizilankhula payekha. +Padakalipano tikulumikizana ndi mabungwe komanso mbali zina momwe tingakonzere msonkhanowu komanso momwe tingapezere mayankho ku mavuto amene tikukumana nawowa, adatero Phiri. +Iye adaonjeza kuti: Zomwe mabungwe ndi anthu onse adzagwirizane ndi zomwe zidzachitidwe chifukwa ife kwathu ndi kupereka mwayi kuti anthu akambirane ndi kupeza mayankho. +Bungweli lidachititsanso msonkhano wotere mu March 2012 pamene kudali chitetezo chokhwima pamene ena amati msonkhanowo udali ndi cholinga chofuna kuthana ndi boma. +Msonkhanowu womwe mbali ya boma sidafikeko, udachitikira ku Limbe Cathedral mumzinda wa Blantyre. +Koma Phiri wati msonkhano ukudzawu umemeza mbali zonse kuphatikizapo a boma chifukwa bungwe lawo limapereka kumva kwa boma lililonse lomwe likulamula. +Koma mkulu wa bungwe loona ufulu wa ogula la Consumer Association of Malawi (Cama) John Kapito wati boma lakhumudwitsa Amalawi chifukwa cholephera kukonza zinthu. +Panopa zinthu zaipa ndipo zasokonekera, makuponi kulibe, chiongola dzanja chakwera ku mabanki zomwe zichititse kuti katundu akwere zomwe zizunze Amalawi. Zomwenso boma likuchita sizikuoneka ndipo tilibenso chiyembekezo ngati zinthu zibwerere mchimake, adatero Kapito. +Iye adati Amalawi akuyenera kumadya mosinira komanso amange malamba chifukwa komwe tikupitaku zinthu zinyanya kuwawa. +Wagolosale ndiye adandipatsa nambala yake Anthuni, njira zophera khoswe nzambiri koma chachikulu khosweyo afe basi. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ena pofuna mkazi amachita kugwa mngongole kuti aoneke ngati, komatu nkhani ya mnyamata wodziwika bwino pa zautolankhani, Vincent Phiri, yemwe sabata yathayi wapanga chinkhoswe ndi okondedwa wake Mable Pikani, sidakhale choncho. +Mnyamatayu akuti kumangika pakamwa kudalipo mpaka adachita kufunsa nambala ya lamya pagolosale yomwe msungwanayo amakonda kugula zinthu ku Ndirande munzinda wa Blantyre komwe onse amakhala. +Akufuna kudzakhala banja lachitsanzo: Mable ndi Vincent Iye adati ngakhale adatenga nambala ya lamyayo, sadayende moyera kufika pomwe alipa kaamba kakuti akatumiza timauthenga ta palamya namwaliyo amayankha mosonyeza kuti alibe chidwi. Koma pali khumbo, njira imakhalapo. +Tsiku lina ndidaganiza zomuimbira ndipo ndidamupempha kuti ngati nkotheka tikumane ndili naye mawu ndipo adandiyankha kuti ngati ndikufuna kukumana naye ndikampeze kwawo, adatero Phiri. +Iye adati posakhalitsa ubale udayambika mpakana kugwirizana za banja chifukwa onse adaona kuti kudalembedwa kuti adzakhalira limodzi mpaka imfa. +Chinkhoswe chidalipo pa 28 November ku Kabula Hill mboma la Blantyre ndipo zokonzekera zili mkati kuti chaka chamawachi adzamange ukwati woyera. +Vincent adati Mable ndi munthu yemwe ali ndi mtima wa mayi, wachikondi, wangwiro komanso wolimbikira ndi wodziwa chomwe akufuna mmoyo mwake. +Naye Mable adati Vincent ndi mnyamata wolimbikira, wamasomphenya ndinso wopanda mtopola ndi anthu. +Pano Vincent ndi woyanganira za momwe malonda akuyendera kukampani ya Finca ndipo akuchita maphunziro a zosunga ndi kubwereketsa ndalama, pomwe Mable ndi namandwa wokonza zovala ndipo ali ndi malo akeake osokeramo zovala. Koma onse awiriwa ndi atolankhani. +Vincent amachokera mmudzi mwa Mkutumula kwa mfumu yaikulu Kwataine ku Ntcheu pomwe Mable amachokera mmudzi mwa Kwachama, mfumu yaikulu Khongoni ku Kasiya mboma la Lilongwe. +Kalonga: Waluso lothetsa makhalu Kunja kuno oimba ndiye mbwee koma luso lawo limakhala losiyanasiyana. Ena ali ndi mawu anthetemya, ena amaimba zipangiso monga zingwenyengwenye, saxophone, ngoma pomwe enanso luso lawo ndi kuthyola sitepe. Koma Innocent Kalonga amathetsa anthu mankhalu ndi luso lake-iye amatha kuimba chida chilichonse mbandi popanda vuto, komanso ndi katswiri pojambula nyimbo. CHIMWEMWE SEFASI adafatsa naye motere: Amatha kuyimba chida chilichonse: karonga Ndikudziwe Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Dzina langa ndine Innocent Kalonga ndimakhala ku Chileka mumzinda wa Blantyre. +Kodi Innocent Kalonga amatani pa Malawi pano? Inetu ndine katswiri wojambula nyimbo zamtundu wina uliwonse kumbali yojambula mawu komanso zithuzi za kanema ndipo ndimapezeka ku Chileka kuno ku Green Arts Studio komwe ndimakhala ndikujambula nyimbo. +Zoti uli ndi luso lojambula udazindikira liti? Ndili ndi zaka 14. Nthawi yatchuthi ndinkakhala ndi chidwi chofuna kudziwa kuti nyimbo amajambula bwanji ndinso kwambiri ndinkakonda kumayesera pakompyuta. Apa mpamene ndidaona kuti zayamba kutheka ndipo padakalipano ndimatha kuimba chida chilichonse chogwiritsidwa ntchito ndi bandi. +Kodi luso la zamaimbidwe pa Malawi likupita patsogolo? Kunena zoona mayimbidwe akupita patsogolo kwambiri moti panopa munthu sungakambe za luso osatchula magulu oimba nyimbo moti masiku ano tikuyenera kuvomereza kuti ku Malawi zoimbaimba zapita ndithu. +Ndi magulu ati omwe wajambulirako nyimbo? Ndajambulako nyimbo za anthu monga Toza Matafale, Wailing Brothers, Limbani Banda ndi anthu ena ambiri, komanso nyimbo zonse zomwe ndidajambula ine palibe anadandaulako. +Kupatula kuimba ndi kupeka nyimbo umapangaso chiyani? Ndimakonda kumvera nyimbo ndipo ndimasangalala kuti takhalapo kalambula bwalo wa oimba amene ndimawakonda. +Ankadzapepesa maliro a mkazi wanga Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Imfa ya mkazi kapena mwamuna wako si mathero amoyo. Mulungu amakoza njira ina kuti akupepese bwinobwino ndipo uyiwale zakale. +Iyi ndiyo nkhani ya momwe Excello Zidana mkonzi wa pologalamu ya Ulimi Walero adakumanirana ndi Keterina Mtambo, mphunzitsi pa Kamalambo FP School kwa Jenda ku Mzimba. +Keterina poyamba adakwatiwa ndi mbusa yemwe adamwalira zaka 7 zapitazo. Nayenso Excello adataya mkazi wake zaka zitatu zapitazo. +Excello ndi Keterina lero ndi banja Awiriwatu adakumana mu November 2013, apa Excello amapita ku Karonga kukagwira ntchito. Monga mkazi wa mbusa, Keterina adali ataiwala za imfa ya mwamuna wake ndipo adayamba kutonthoza Excello paimfa ya mkazi wake. +Kupatula kutonthoza, Keterina adalimbikitsa Excello ndi mawu a Mulungu, osadziwa kuti mawa awiriwa atonthozana zenizeni pokhala mayi ndi bambo Zidana. +Kuchoka apo, awiriwa akuti adagawana manambala kuti azilimbikitsana komanso kuchezerana kufikira mu January 2015 pamene nkhani idasintha. Chikondi chidayamba kumera pamtima pa aliyense, kodi Mulungu akufuna titani? Mu March 2015, ndidaganiza zomuyendera, kukangozindikira kuti ali ndi chilichonse chomwe ndimafuna..nditadzamuyenderanso mu May 2015, ohndiye mtima wanga kuferatu chifukwanso patsikulo adandikonzera nkhomaliro. +Basitu Keterina adangoti zitero monga momwe mukufunira.zonse zidatheka kuti basi tizikapepesana tokha pakuti tonse tidakumana ndi mavuto, adatero Zidana. +Pamene amakumana nkuti aliyense ali ndi ana atatu, pano poti awiriwa ndi thupi limodzi ndiye kuti banjali lili ndi ana 6 omwe ati akumvana motheratu. +Chinkhoswe chidachitika mu July ndipo ukwati wachitika pa 1 November, 2015 ku Likuni mumzinda wa Lilongwe. +Keterina amachokera mmudzi mwa Namasasa kwa T/A Mwabulambya ku Chitipa. Excello ndi wa mmudzi mwa Mtherereka T/A Namkumba mboma la Mangochi. +Kulimbana ndi alaliki Ndidakhala pa Wenela tsikulo kubwira mpweya, uku ndikuitanira basi. +Ndirande iyi! Machinjiri iyo! Ntcheu-Balaka cha uko!!! ndidali kutero. +Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Pajatu masiku ena ndikati ndilowe three engine, kuitanira basi zitatu nthawi imodzi zimatheka. +Ya Ntcheu-Balaka ija itadzaza, ndidapita ndikatenge zanga. Kaya ikafika ku Balaka ndilibe nazo ntchito. Ngakhale itapezeka kuti pofika pa Mdeka mwangotsala anthu atatu, zingandikhudze? Nditafika uko ndidapeza munthu wa Mulungu akulalikira, keupempherera apaulendo kuti ayende bwino. +Ndikunena pano ziwanda za pamsewu zakonzeka kukulikhani. Ziwanda za pa Linthipe zakonzeka kumwa magazi anu ngati simutetezedwa. Inde ziwanda zochoka pansi pa madzi zikusautsani ngati simulapa, adali kutero mlaliki. +Abale anzanga, ulaliki wamtundu wanji uwu wokhala ngati amalankhula nazo ziwanda? Kodi mlaliki ameneyu atati wakatumikira kuchipatala, sanganene kuti: Inu ochimwa inu! Lapani lero lino nditi lapana. Ngati simutero, zifuwa zanuzo zikutengerani kugahena. Kuchita kusaweruzika kwanuko, wa kumoto basi. +Ndi mwayi omwe kuti utumiki wa kuchipatala udamusempha. Kodi sindinganene kuti akuopa kuti kuchipatalako sakatulukako ndi loboola ilo amapeza pano pa Wenela? Nkhani ya alaliki ili mkamwamkamwa ndi ya mlaliki Makala Funeral. Mumudziwa bwino woimba uja ankakamba za mfumu Betisezala ndi zolembalemba pakhoma. Tikumva kuti zinavutatu uko ku Mangalande. +Mwachidule, zikumveka kuti mlaliki adacheza ndi mnzake wa Abiti Patuma wina pangongole ndiye lero nkhani yonse ili pa mbalambanda. +Akungomulakwira mlaliki. Tikudziwa ankamwa, kusuta mpaka kugona mchimbudzi kalelo koma anali asanalape. Lero taonani nkhani zikuphulikazi! adatero Abiti Patuma titakhala malo aja timakonda pa Wenela madzulo a tsikulo. +Apa nkuti akundionetsa zithunzi ndi mavidiyo pafoni yake akuonetsa chikondi cha mlaliki ndi uyu msangwana wa kwa Msamati. +Nkhanizi zikumavuta kuyankhira. Kukhala ngati chiwanda choipa chalowa pamudzi pano. Taonani mudabweretsa za uyu wojambula mizimu, wopalasa mlengalenga, naye uyu wa matama ndi galimoto zake! Tsono mukutinso bwanji za mlaliki wathu wa ku Chilomoni? adafunsa Gervazzio. +Musandifunse kuti nkhaniyi imayenda bwanji chifukwa nanenso sindikudziwa. Chomwe ndikudziwiratu nchakuti awa ndi masiku otsiriza ndipo kuyalutsa anthu a Mulungu ana a njoka ena akuchitenga cha fasho. +Atentha nyumba kaamba ka K2 000 Mkulu wina ku Ntchisi waona mbwadza atagamulidwa kuti akaseweze zaka 8 kundende kaamba kobutsa nyumba ya mnzake chifukwa cha ngongole ya K2 000. +Escom in free-for-all fuel scam Wait gets longer Secrecy over party funders Bwalo la milandu ku Ntchisi pa 27 November lidalamula Thokozani Paul, wa zaka 21, yemwe amachokera mmudzi mwa Mdaopamudzi mdera la T/A Nthondo mbomali kuti akagwire ntchito yakalavulagaga kaamba koyatsa nyumba ya nyumba ya Winston Njirisi, wa zaka 39. +Woimira boma pamilandu, Sergeant Austin Daudi, adauza bwaloli kuti bamboyu, yemwe ali pabanja komanso ali ndi ana, adapalamula mlanduwu usiku wa pa 21 November pamudzi wa Chimbaka mdera la Nthondo lomwelo. +Malingana ndi Daudi, Njirisi akuti adali ndi ngongole ya K2 000 ya womangidwayu yomwe ankafuna kugulira ndowa ya chimanga. +Wodandaula adalephera kupereka ndowa ya chimanga kwa womangidwawa komanso kubweza K2 000, zomwe zidakwiyitsa omangidwawa. +Patsikulo onse awiri adapita kukamwa mowa ndipo ali komweko mkangano udabuka kaamba ka ngongoleyo ndipo mkanganowo udakafika mpakana kunyumba ya wodandaulayu, adatero Daudi. +Iye adati cha mma 7 koloko usiku Paul adanyamuka kunyumba ya Njirisi kupita kunyumba kwake ndipo patangodutsa mphindi makumi atatu, adabwerera ndi cholinga chokabutsa nyumba ya mnzakeyo ndipo panthawiyo nkuti Njirisi akugona mnyumbamo ndi banja lake pomwe nyumbayi imayaka. Adapulumuka kaamba ka kukuwa kwa anthu amene adaona nyumbayo ikuyaka ndipo adathawira panja atangopulumutsamo chitenje chimodzi ndi masikito. +Atakaonekera kukhoti pa 27 November, Paul adapezeka wolakwa pamlandu wotentha nyumba motsutsana ndi gawo 337 la malamulo a dziko lino. +Popereka chigamulo, majisitireti Dorothy Kalua adati mlanduwu ndi waukulu potengera kuti wodandaulayo adamusiya padzuwa popeza nyumba ndi katundu wambiri adapsera momwemo. +Zasokonekera ku kapitolo Zili kukapitolo ku Lilongwe si ndizo. Pomwe apolisi achilimika kugwira ndi kutsekera galimoto zopezeka ndi milandu, oyendetsa minibasi agangalama ndipo anenetsa kuti zikaonjeza, apanga zionetsero zosonyeza mkwiyo wawo. +Escom in free-for-all fuel scam Wait gets longer Secrecy over party funders Sabata yatha yokhayi kuyambira Lolemba kufinka Lachitatu kudali mulu wa galimoto kulikulu la polisi mumzindawu ku Area 3 ndipo chiwerengero cha minibasi zokha chimaposa 300. +Nantindi wa oyendetsa basi ndi otolera ndalama udalinso komweko Lachiwiri pomwe Msangulutso udakazungulirako, mkwiyo utalemba tsinya pamphumi zawo kusonyeza kusakondwa ndi zomwe zikuchitikazo. +Ena mwa minibasi omwe adatsekeredwa kupolisi ya ku Area 3 Madiraiva ena adati samamvetsa chomwe adagwidwira ndipo adati ngati zotere zingapitirire, nawo aona njira zawo. +Taganizani munthu kukugwira mmawa mpaka pano 2 koloko akukana kuti ulipire uzipita kokapanga bizinesi. Mmesa munthu akakugwira umayenera kulipira mlandu wako ndi kukuuza zoti ukachite usadabwerere pamsewu? adatero mmodzi mwa oyendetsa basizo, Valeson Gilbert. +Mosatsutsa kuti akusungadi basizo ndi galimoto zina, apolisi adati akuchita izi ngati njira imodzi yofuna kuchepetsa ngozi mumzindawu panyengo ino ya zisangalalo za Khrisimasi ndi Nyuwere. +Mneneri wa apolisi mchigawochi, Ramsey Mushani, adati apolisi sagona mpaka ataonetsetsa kuti galimoto zokhazo zomwe ndi zoyenera kuyenda pamsewu ndizo zikuyenda komanso kuti galimoto zonyamula anthu monga basi ndi minibasi zikutsata mlingo woyenera wa anthu okwera. +Mwina anthu akhoza kumaona ngati tikukhomerera anthu wamba, koma ayi. Kuti mufufuze eni basi ndi galimoto zimene tikusunga muona kuti zina eni ake ndi apolisi, asirikali ndi akuluakulu a mboma. +Cholinga chathu nchakuti ngozi zichepe chifukwa nyengo ngati ino anthu amafuna kukokera ndalama za chisangalalo ndiye amatulutsa galimoto iliyonse yabwino ndi yoipa yomwe, zomwe zimachulutsa ngozi pamsewu, adatero Mushani. +Momwe nthawi imati 6 koloko mmawa Lolemba, apolisi apamsewu adali atafika kale ndipo ataunjika kale basi ndi galimoto zambiri zomwe zidachititsa kuti chiwerengero cha basi chichepe ndipo mtengo wokwerera basi ukwere. +Anthu ambiri tsikuli adachedwa kutchito zawo chifukwa chosowa mayendedwe mpakana ena amasuti awo adakwera malole kuopa kupalamula kuntchito. +Ena mwa anthu omwe adalankhula ndi Msangulutso adati sakudandaula ndi zomwe apolisi akuchitazo chifukwa akuteteza miyoyo yawo koma adadandaula kuti apolisiwo akagwira basi, amatsitsira anthu panjira zomwe zimawasokoneza. +Ntchitoyi ndi yabwino chifukwa akuteteza ife tomwe koma vuto lili pakuti akagwira basi amatitsitsira panjira poti kupeza basi ina nkovuta. Zikadakhala bwino akadati azimuuza wa basiyo kuti akatsitse anthu kenako nkumutenga. +Tidavutika ife dzulo (Lolemba) timachoka ku Area 49 ndipo adatitsitsira pa Ntandire poti kukwera basi ina nkovuta chifukwa zimadutsa zodzadza kale mpaka tidachedwa kuntchito, adatero Moses Chiumia, yemwe amagwira ntchito ku khonsolo ya mzindawu. +Oyendetsa basiwo adatinso pena akumadabwa kuti ulendo umodzi akulipitsidwa kangapo pomwe iwo amadziwa kuti ukalakwa ulendo umodzi nkulipira suyenera kulipiranso pokhapokha ngati wakanyamukanso ulendo wina. +Mchitidwewu wachititsa kuti njira zammakwalala zomwe anthu ndi njinga zokha zimadutsa, muyambe kuyenda basi ndi galimoto zolakwa kuthawa kugwidwa ndi apolisi. +Izi zadzetsa nkhawa kumakolo kuti basi ndi galimoto zotere zikhoza kuwaphera ana omwe amakhala akusewera mmakwalalamo. +Njira zomwe akudutsazo nzoopsa chifukwa makona ake ngosaonekera patali, mulibe zikwangwani komanso ana adazolowera kuseweramo ndiye mwatsoka wina adzati akhote nkukumana ndi mwana, adatero Amina Gibson wa ku Area 36 muzindawu. +Milandu yambiri yomwe ikupezeka ndi yoyendetsa galimoto popanda chiphaso, galimoto zopanda mapepala oyendera pamsewu, matayala akutha ndi kunyamula anthu opitirira muyeso wa galimoto. +Sabata ziwiri zapitazo apolisi mumzinda wa Blantyre adachitanso chimodzimodzi moti nakoso kudali pokopoko mpaka madaraiva a minibasi kuchita zionetsero pofuna kuumiriza apolisi kuti awapatse galimoto zawo koma adawabalalitsa ndi utsi wokhetsa msozi. +The Rain: Mnyamata wanthetemya Anthu ambiri otchuka makamaka amasewero, oyimba ndi azisudzo amakonda kudzitcha maina otchukira kusiya awo a pamchombo. Mchitidwewu sudayambire kuno ku Malawi, ayi, koma ngakhalenso kumaiko akunja ziliko. Tikakamba za kwathu kuno tili nawo maulendo a Soldier, Anonga, Piksy, Shakira, Safintra ndi ena. Omwe atchulidwa apawa ndi zitsanzo chabe koma alipo ambiri makamaka achinyamata omwe akutchuka ndi nyimbo zamakonowa. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Bright Vitsotso, mnyamata yemwe watchuka pawailesi ndi kanema ndi nyimbo zamakono ndipo iye akuti dzina lake lodyera ndi The Rain. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Vitsotso: Ndimagawa nthawi yanga Tandifotokozera kuti ndiwe ndani mnyamata. +Dzina langa ndi Bright Vitsotso wa kwa Waliranji mboma la Mchinji, koma ndikukhala ku Lilongwe. +Wati Bright Vitsotso, nanga The Rain akuchoka pati? The Rain ndi dzina lomwe ndimatchuka nalo pazoimbaimba. Pali maina awiri la The Rain ndi Young Star omwe anthu otsata nyimbo zanga amadziwa. +Umaimba chamba chanji? Ndimaphatikiza Rap ndi Hip Hop zomwe ndimaziimba motsatira mingoli ya Chifirika. Panopa ndidapanga chikole ndi kampani yojambula nyimbo ya Dash Travellers Entertainment ndipo ndikugwira nawo bwino kwambiri ntchitoyi. +Luso lako lidayamba liti? Chilakolako choimba chidandiyamba mchaka cha 2005 pomwe ndinkaimba ndi anzanga koma zidali ngati zamasewera chabe. Ndikukula ndidayamba kulemba nyimbo zokhudza zinthu zochitikadi mmoyo wa munthu nkumayeserera kuziimba uku ndikudzijambula ndekha nkuona kuti zikumveka bwino ndithu. +Pakalipano uli ndi nyimbo zingati? Ndili ndi nyimbo zingapo, yoyamba kujambula idali Chikumbuntima yomwendidathandizana ndi Peter Banda ndi Mabilinganya Empire. Kenako ndidajambula Swazi ndi Mabilinganya Empire kenako Honey yomwe ndidajambula ndi Katelele Chingoma. Nditangomaliza imeneyi ndidajambula Ndikuopa ndi Lady Pace nkupuma kaye. +Nyimbo zako zimakhala ndi uthenga wanji? Nyimbo zanga zimakamba za mmene moyo ulili ndi nkhani zochitikadi. Sindifuna kuimba nyimbo zokhala ngati nthano, ayi, koma zoti munthu akamamvera azitha kulumikiza zomwe ndikunena ndi zomwe amakuna nazo kapena kuona mmoyo. +Kupatula zoimba, china chomwe umachita ndi chiyani? Kupatula kuimba ndimalembanso mafilimu, kuvina, kusewera mpira komanso ndidapanga za magetsi ku Yunivesite ya Nairobi ku Kenya kenako ndidagwirapo ntchito mmapolojekiti a Airtel kwa zaka 5 koma pano ndikupitiriza maphunziro ku United Arab Emirates. +Luanar ikhazikitsa magulu a alimi akafukufuku Nthambi ya zaulangizi pasukulu yaukachenjede ya Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) sabata zapitazo idakhazikitsa magulu a alimi a kafukufuku. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Magulu a alimiwa akhazikitsidwa ndi cholinga chopereka mwayi kwa alimi kuti atengepo mbali pa kafukufuku kuti apeze mayankho a mavuto omwe akukumana nawo paulimi. +Kwa nthawi yaitali, alimi akhala akungolandira zotsatira za kafukufuku kuchokera kwa akatswiri a kafukufuku ndi alangizi. Izi zapangitsa kuti alimi azingolandira chilichonse kaya ndi chogwirizana ndi kudera kwawo kapena ayi kotero kukhazikitsidwa kwa maguluwa kuthandiza alimiwo kupeza mayankho a mavuto a ulimi mmadera awo. +Ntchitoyi ndi ya zaka zinayi ndipo ikuchitika kudzera mupulojeketi ya Best Bets III ndi chithandizo chochokera ku McKnight Foundation. Magulu a alimi akafukufukuwa akhazikitsidwa mmadera a zaulimi a Zombwe mboma la Mzimba, Mkanakhoti ku Kasungu ndi Kandeu ku Ntcheu. +Ena mwa alimi otenga nawo gawo pa chilinganizochi Malingana ndi yemwe akutsogolera ntchtitoyi, Daimon Kambewa, kwa nthawi yaitali alimi akhala akutengedwa ngati osadziwa chilichinse kotero akatswri akhala akupanga kafukufuku paokha ndi kumawauza alimi kuti atsatire zomwe apeza. Izi zachititsa alimi kumangotsatira zilizonse ndipo njira zina sizinathandize kutukula ulimi. +Kutengapo mbali pa kafukufuku kuthandiza alimi kukhala ndi luntha ndi chidwi choganiza ndi kupeza njira zomwe zingawathandize kuthetsa mavuto awo paulimi mogwirizana ndi madera awo. +Kwanthawi yaitali akatswiri a zaulimi akhala akupanga kafukufuku wawo paokha ndi kumawauza alimi zoti achite ndipo izi zapangitsa alimi kumangodikira alangizi kuti abweretse njira zatsopano za ulimi. Ntchito yopanga kafukufuku limodzi ndi alimi ithandiza kulimbikitsa kudzidalira komanso kukhala ndi luntha, luso ndi chidwi chithetsa mavuto a ulimi paokha, adatero Kambewa. +Gulu lililonse lili ndi anthu 22 ndipo anthuwo asankhidwa ndi anthu a mmadera awo potengera chidwi chawo poyesera luso lamakono paulimi. Membala aliyense wa gulu akhala ndi munda wa chionetsero koma azikumana ndi kumakambirana nagawana nzeru. +Alimiwa aziyenderana mminda ya wina ndi mnzake kuti aziphunzitsana ndi kumalimbikitsana. +Ntchitoyi ikuyembekezeka kuthandiza alimi kukhala anthu oganiza mozama pofuna kuthetsa mavuto omwe akukumana nawo paulimi ndipo zichepetsa mchitidwe wodalira kapena kudikira alangizi kuti awauze njira zothetsera mavuto awo popeza alangizi alipo ochepa kuyerekeza ndi alimi. +Khama lipindula paulimiPhungu Nthawi zambiri chomwe chimasowa paulimi ndimasomphenya. Alimi ambiri amangolingalira zoti ndikakolola chaka chino ndidzalimanso chaka cha mawa mmalo moti azilingalira kuti chaka chino ndalima ndipo chaka chamawa ndidzakhale pena. Phungu wa kunyumba yamalamulo wa ku mpoto kwa boma la Mangochi Benedicto Nsomba ndichitsanzo chabwino pankhaniyi. Iye adayamba ngati mlimi ochulukitsa mbeu nkusuntha kufika pogulitsa mbeu ndipo pano ali ndi kampani yakeyake yopanga mbeu. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere: Nsomba: Mbewu zanga nzovomerezeka ndi boma Ndikudziweni olemekezeka. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ine ndine Benedicto Chambo ndipo, monga mwanena kale, ndine phungu wa ku Nyumba ya Malamulo woimira anthu a kumpoto kwa boma la Mangochi. Kunyumba ya Malamuloko ndilinso mukomiti ya zaulimi komanso pandekha ndimalima kwambiri. +Inu mulinso ndi kampani yopanga mbewu, kodi mbiri yanu ndi yotani? Za inetu anthu ambiri sakhulupirira ayi. Ndidayamba zaulimi ngati mlimi wochulukitsa mbewu pansi pa gulu la Association of Smallholder Seed Multipliers Action Group mchaka cha 2005. Nditachitapo ulimiwu ndidasuntha nkuyamba kugulitsa mbewu nditatsegula Chambo Agro- Dealers ku Mangochi komweko. Ndagulitsa mbewu mpaka kufika pomwe ndimatsegula kampani yanga yopanga mbewu ya Pindulani Seed Company. +Chiyambi chake nchotani? Mchaka cha 2010 ndidaona kuperewera kwa mbewu za gulu la nyemba pamsika ndiye ndidaganiza zoyamba kupanga mbeuzi. Ndapangapo mbewu za mgulu la nyemba kwa zaka ziwiri mpaka kufikira mchaka cha 2013 pomwe ndidaonjezera nkuyamba kupanganso mbewu ya chimanga kufikira pano. +Muli ndi msika wa mbewu zanu? Kwambiri ndipo mbewu zanga ndi zimodzi mwa mbewu zomwe alimi ambiri akukonda chifukwa zimamera ndi kubereka mwapamwamba kwambiri. Mwinanso ndikuuzeni pano kuti boma lidavomereza mbewu zanga moti pano zili mupologalamu ya zipangizo zotsika mtengo ya sabuside. Apa ndikutanthauza kuti mbewu ina yomwe alimi alime kuchokera musabuside ya mgulu la nyemba komanso chimanga ndi yopangidwa ndi kampani yanga ya Pindulani. +Mumapanga mbewu yochuluka bwanji pachaka? Poyamba penipeni ndidayamba ndi matani 10 okha ndipo ndimanka ndikukwera pangonopangono mpaka pano ndidakula ndithu. Chaka chino ndapanga matani 340 a mbewu zosiyanasiyana za mgulu la nyemba ndinso matani 150 a chimanga chamakono chopirira ku ngamba chomwe boma ndi akatswiri akulimbikitsa. Ndili wokondwa kuti mbewu zonsezi zidatengedwa mupologalamu ya sabuside. +Inu mbewu zanu mumazitenga kuti? Si njere iliyonse yomwe ili mbewu. +Nzoona, si njere iliyonse ungabzale nkumati ndi mbewu. Ine ndili ndi alimi anga ochokera kudera langa omwe ndimagwira nawo ntchito. Ndimawapatsa mbewu kuti achulukitse ndipo ndimawagula pamtengo wabwino ngati njira imodzi yowatukulira. Alimi ambiri panopa kudera kwanga adatukuka moti amangamanga nyumba zamakono za malata kumeneko kuchokera mu ntchito imeneyi. +Tinene kuti mudaima pambewu zamitundu iwiriyi basi? Ayi, ndiye kuti mutu wasiya kuganiza. Lingalirani komwe ndikuchokera kudzafika pano ndiye ndiimire pano? Pakalipano tikuchita kafukufuku wa mbewu za mtedza ndi nyemba zoyenera mthirira zomwe zotsatira zake zikatuluka tikhala tikulimbikitsa alimi kuti azichita ulimi wamthirira wa mbewuzi. Kupatula apo, tikuchitanso katupe wa mbewu zamakono za chinangwa ndi mbatata zamthirira moti ntchito imeneyi yakhala pangono kutha kuti tiyambe kugulitsa mbewu yake. +Eni makampani opanga ndi kugulitsa mbewu amadandaula za akamberembere omwe amakopera mbewu zawo nkumaononga mbiri yawo, kaya inu mudakumanapo nazo zotere? Zimenezo nzoona, akamberembere alipodi koma chimachititsa kwambiri ndi ogwira ntchito kumakampaniko omwe ali osakhulupirika chifukwa ndiwo amatenga mapaketi nkumakagulitsa kwa akamberemberewo kuti aziikamo mbewu yachinyengo. Komabe pobwerera kufunso lanu, ife zimenezi sitidakumanepo nazo chifukwa tidapanga njira yoti mapepala a umboni aja amati seal oika mkati mwa paketi, timapanga tokha ndiye olo atapeza mapaketi athu, seal ikhoza kuwasowa. +Alimi ambiri amakakamira pamodzimodzi zaka nkumapita, inu mungawauzenji? Nkhani yaikulu ndi kukhala ndi masomphenya basi. Kumaona patali kuti kodi ineyo lero ndili pano nanga mawa ndidzakhale pati? Mlimi akakhala ndi maganizo otere, zinthu zimayenda chifukwa amayesetsa kuti maloto ake aja akwaniritsidwe, asafere mmalere. China, pamafunika kulimba mtima pochita zinthu chifukwa ukakhala ndi mantha ndiye sizingakuyendere mpangono pomwe. +Kupatula kuyendetsa kampani ya mbewu, pali china chokhudza ulimi chomwe mumapanga? Ndili ndi sikimu zingapo ku Mangochi komwe ndimachitirako ulimi wamthirira wa mbewu zosiyanasiyana. Ndidalemba alimi oposa 1 500 nkuwagawira malo musikimumo kuti azilima. Akakolola, ndimawagula mbewuzo pamtengo wabwino komanso zina zimakhala zawo zakudya pakhomo. Mwezi wa October alimi adakolola nyemba zambiri ndipo ndidawagula zonse pamtengo wa K600 pakilogalamu moti pano ambiri ali ndi ndalama, savutika nyengo yachisangalaloyi. +Adona Hilida akadangobwera Ngakhale pa Wenela padali zovuta, malo aja timakonda padali kuphulika nyimbo. +Ine nilibe pulobulemu Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Nilibe pulobulemu. +Chifukwatu timayembekezera kuti wotisiyayo mtembo wake ufika masana a tsiku limenelo. +Titakhala pamalopo, adabwera mkulu wina akuthamanga. +Akuluakulu,tiyeni mukandithandize kukhazikitsa mtima pansi bambo a malemu, akufika kumene kuchokera kwawo kwa Govala, adatero mkulu uja, thukuta lochita kusamba. +Tidakhamukira komweko! Koma mkulu adavuta. +Mwana wanga Boyisi waferanji? Boyisi anditumizira bulangete kuchoka ku Joni ndani? Ndikuti osandigwira! adali kulira mkuluyo. +Pepani, pepani, wina ankayesera kumutonthoza. +Mkulu adali ndi mavuvu! Osandigwira! Boyisi waferanji mwana wanga? Bwanji sunandifonere kuti unditsanzike? Osandigwira ineeeeee! Anthu okwana 10 adakwanitsa kumukhazika pansi. Adali kufwenthera ndipo ine ndidakhala moyandikana naye. +Mwamwa kale tiyi? adandinongoneza mkuluyo. +Abale anzanga, matchona amayenera kubwera kumudzi akakhalakhala kunjako. +Nkhani idayala nthenje pa Wenela usiku umenewo kusiwa idali ya matchona. +Koma mtchona wamkulu ndi Adona Hilida! Makhrisimasi awiri ndithu ali mliyenda! Ndalama ali nazo, adatero Gervazzio. +Ali ku exile! Anyamata ambiri amakhala ku exile asanalande ulamuliro koma Adona Hilida adathawira kunja ulamuliro utawasempha, ntchito za manja awo poboola mipopi ya chuma zitawachitira umboni, adatero Abiti Patuma. +Muli ndi umboni wanji kuti zikuwakhudza? Mudaliko? adafunsa mkulu amene adali naye tsiku limenelo. +Mufunanso umboni wotani kuposa zomwe zikuonekeratuzi? Adathawiranji? Nanga anthu onse akuwatchula Adona Hilidawa angakhale kuti akulota? adayankha Abiti Patuma. +Abale anzanga, inetu zimandisempha. +Ndipo akadangobwera nthawi ya Khrisimasiyi chifukwatu ndiye chochita sangachisowe. Akhoza kumagulitsa nawo mabaluni ngakhalenso makombola awandawa. Chochita sichingasowe, adatero Gervazzio. +Komanso anthu onsewa akuti ndalamazo zidali zakuti Polisi Palibe idzaluzire mpando wonona. Onsewa ngamisala? Akuopa chiyani Adona Hilida? Akadangobwera kuti mlandu wa munda tidzaukambire pamunda pawo pomwepo, adatero Abiti Patuma. +Kwa ine, ndingothokoza kuti sindili mtchona ngati Adona Hilida. Ndimapuma mpweya mopanda kucheuka! Kusankha nkwanga kuti ndisangalale Khrisimasi kapena ayi. Pajatu kwathu kwa Kanduku timakhulupirira kuti chisangalalo cha Khrisimasi chidalipo kuyambira kale, Yesu asadabadwe. +Koma izotu sindizitengera kwenikweni pozindikira kuti uzimu ndiwo ufunika. +Sindikulalikira, koma ndi bwino kuthokoza kuti taonanso Khrisimasi ina! Ndi bwino kumayamika Mulungu chifukwa mwamwayi nkutsetserekera mu 2016. Zaka ndiye zikukhamukira ku 2019 kuti tidzaone Adona Hilida ndi Polisi Palibe akuthotha Moya Pete ndi Dizilo Petulo Palibe. +Aphungu adzuma ndi kagawidwe ka makuponi Ganizo la boma loyamba kugawa makuponi ogulira zipangizo za ulimi zotsika mtengo mupologalamu ya sabuside lalandilidwa ndi maganizo osiyanasiyana pakati pa aphungu a ku Nyumba ya Malamulo, mafumu ndi Amalawi ena. +Kauniuni wa Tamvani wapeza kuti pomwe boma lili ndi maganizo oyamba kugawa makuponiwa mchigawo cha kummwera, anthu ali ndi maganizo ena makamaka polingalira kuti mvula ili pakhomo mzigawo zonse. +Escom in free-for-all fuel scam Wait gets longer Secrecy over party funders Lachinayi lapitali mudali chisokonezo mNyumba ya Malamulo ku Lilongwe pomwe aphungu amafuna kuti boma lilongosole momveka bwino cholinga choyamba kugawa makuponi kummwera. +Nkhani inakula mNyumba ya Malamulo ndi ya makuponi Phungu wa kumadzulo kwa boma la Mzimba Harry Mkandawire ndiye adatokosa nkhaniyi ponena kuti anthu a mboma lake akufunika makuponi ogulira zipangizo zaulimi msanga chifukwa mvula idagwa kale ndipo anthu akudikira kudzala. +Nchifukwa chiyani mwasankha kuyambira kummwera pomwe mvula yayamba kale mmaboma ambiri mzigawo zonse? Pamenepa pali mafunso ambiri ofunika mulongosole bwino,adatero Mkandawire. +adakhazikike, aphungu ambiri adaimirira pofuna kuonetsa kusakhutira kwawo ndi ganizoli mpaka nduna ya zachuma Goodall Gondwe, yemwe amayankha mmalo mwa nduna ya zamalimidwe, Allan Chiyembekeza, adavomereza kuti ndondomeko ya sabuside idalakwika. +Gondwe adati ganizo loyamba kugawa makuponi ku mmwera lidadza polingalira kuti nthawi zambiri mvula imayambira mchigawochi pakudza. +Si kuti pali mangawa alionse, ayi, koma monga tikudziwa, chaka ndi chaka mvula imayambira kummwera ikamabwera nchifukwa tidaganiza zoyambira kumeneko, adatero Gondwe. +Yankholi silidagwire mtima aphunguwo ndipo adadzudzula boma chifukwa cholephera kukonzekera mokwanira mupologalamuyi. +Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe omwe amakhudzidwa ndi nkhani za ulimi wa Civil Society Agriculture Network (Cisanet) Tamani Nkhono-Mvula adati ngakhale kuti nchizolowezi kuyambira kummwera kugawa makuponi, chaka chino chokha ndondomeko ikadasintha. +Iye adati boma lachedwa pachilichonse mundondomekoyi ndiye sipakufunika kutsatira za mmbuyo koma kupeza njira zomwe zingagwirizane ndi momwe zinthu zilili. +Chiyambireni, boma silidakonzekere bwino ndondomekoyi. Pena pake tikhoza kuwamvetsetsa kuti pali mavuto a zachuma koma adadziwa kalekale zimenezi ndipo pano amayenera kukhala ndi njira, adatero Mvula. +Iye adati chomwe boma likadachita nkuthamangitsa chilichonse kuti makuponi afikire mmadera onse kuti mvula ikamayamba alimi asadzazingwe nthawi yothaitha. +Akuganiza bwanji poti nthawi yatha kale? Mavuto a zachuma ali apo, akadapanga zoti makuponi apezeke msanga ndipo anthu alandire mzigawo zonse msanga. +Kunjaku kuli kale njala ndipo ngati sitisamala, chaka cha mawa kukhoza kudzakhala zovuta zenizeni chifukwa alimi ambiri amadalira sabuside ndipo mmadera momwe anthu amalima kwambiri, mvula idagwa kale koma sali ku mmwera, adatero Mvula. +Paramount Chief Lundu wa mboma la Chikwawa adati mmadera ambiri mchigawo cha pakati mvula idagwa kale ndipo anthu akungoyembekeza kubzala. +Iye adati kuchedwetsa makuponi kupangitsa kuti anthu adzalandire mochedwa zomwe zingachititse kuti mbewu zawo zidzasemphane ndi mvula monga momwe zidalili chaka chatha. +Akadangoti tochepa tomweto agawe dziko lonse kuti mzigawo zonse anthu ena abzaleko osati mchigawo chimodzi chokha chifukwa sitikudziwanso kuti makuponi enawo afika liti ndipo adzafika angati, adatero Lundu. +Paramount Chief Kyungu wa ku Karonga adati kwa iye nkhani yaikulu padakalipano ndi chakudya osati makuponi monga momwe anthu ena akunenera. +Iye adati mvula sidanunkhire mmaboma ambiri mchigawochi ndiye palibe kanthu komwe angayambire chachikulu anthu apeze chakudya basi, adatero Kyungu. +T/A Mkanda wa ku Mulanje adati iye ndi wokondwa kuti makuponi afika tsopano mdera lake ndipo akudikira kuti mvula ikagwa anthu akabzale mbewu mminda mwawo. +Zochitika mminibasi Tsikulo pa Wenela padalibe zomvera nyimbo. Nanga abale anzanga, anthu akuluakulu ngati ife tingamamvere nyimbo monga Tsika Msungwana Tsika? Nanga inu mungamvere nyimbo ija ya Msati Mseke. Za nyimbo imeneyi ndidamva kwa Gervazzio, amene akuti sangayerekeze kuika pamalo paja timakonda pa Wenela. +Amavala zigoba.Amadzipaka matope. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Uku ndiye timati kufwala gule, kuulula vilombo. Adamuuza ndani kuti amachita kuvala? Kukadakhala kwathu ku Thiwi ku Nkhotakota, tikadacheza mwana uyu, adatero Gervazzio. +Tsono tsiku limenelo kudali kuonera mafilimu a ku Nigeria. Pajatu ine mafilimu amenewa ndidaimika manja kalekale kuti sindidzaoneranso, amataitsa nthawi. Zoona filimu izikhala yoonetsa munthu akuliza galimoto, kudzaponda kuti vruuuu! Kenako kuyamba kuitana wapageti kuti akatsegule. Akatero wageti kulimbana ndi geti. Kenako ndiye kuti muonera mphindi zisanu mkuluyo akuyendetsa galimoto. +Koma filimu imene tinkaonera tsikulo ndiyo yandichititsa kuti ndilekeretu kuonera filimuzi. Ngakhale wina atandithira Doom mkamwa, sindingachite. Mfilimuyo mkazi wina adafuna kupha mwamuna wake kuti atenge chuma chake. Iye adaphika chakudya ndipo adathiramo tameki. Kuti adziwe kuti tamekiyo wakolera mayiyo adalawa chakudyacho! Tsiku lotsatira, wa minibasi ina adati akufuna agwire ntchito ina ndipo adandipempha kuti ndiyendetse mmalo mwake. Ndidaima pa Wenela uku wina akuitanira. Ndirande! Ndirande! Ndirande awiri a chamba! Awiri a change muno ku Ndirande! adali kutero. +Nthawiyo nkuti ndikukhoma marivesi, kudzapititsa patsogolo pangono. +Mpando woyandikana ndi ine padakhala mkulu wina ndipo kuchitseko kudali msungwana wina amene anali ndi foni yake mmanja. Iye adali ndi chikwama chija amachitcha mwina ndi wokagona pamiyendo pake. +Chomwe chinkandichititsa chidwi chidali chakuti bamboo uja ankasunzumira zomwe msungwana amalemba pafonipo. Pena mzibamboyo amaseka nawo nkhani za msungwanayo. Ndikhulupirira idali Whatsapp imeneyo. +Mtsikana uja adaoneka kuti amanyansidwa ndi zochita za bamboo uja. Bamboyo adali kunjoya zolemba za msungwana uja. +Kenako, tikuyandikira pa Chimsewu mzibambo uja adayamba kukuwa. Njoka! Njoka! Njoka! adadumpha ndipo adachititsa kuti ndisiye chiwongolero. Pomwe ndimadzachigwiranso, nkuti minibasi ikutaya msewu. +Mayo ine ngozi iyi! Ngozi iyi! ena adali kukuwa. +In the name of Jesus! In the name of Jesus! enanso adali kukuwa. +Mwa chisomo, ndidakwanitsa kuimitsa minibasi ija. Padalibe wovulala. Koma bamboo uja adatsegula chitseko ngakhale adali pakati. Adamudumpha mstikana uja nkutuluka panja. +Adali kukuwa: Njoka! Njoka! Mchikwama! Njoka! Msungwana uja adali kuseka chikhakhali. +Bamboyu amawerenga mauthenga anga, ndiye ndimafuna asiye kuwerenga mauthenga a eni. Ndinangolemba uthenga uwu, adatero akundiwerengetsa uthenga wopita kwa bwenzi lakewo. +Ndili mminibasi koma abambo ndayandikana nawo akungowerenga mauthenga anga. Sakudziwa mchikwamamu muli njoka. +Kasambara: Kulimbikitsa anthu mkuimba Martha Kasambara ndi woimba nyimbo za uzimu wokhala ku Mzuzu. Iye ali ndi zimbale ziwiri ndipo mu December chaka chino adzakhazikitsa chimbale chake chatsopano chotchedwa Amasamala. Mtolankhani wathu DAILES BANDA adacheza naye motere: Tikudziweni. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndine Martha Kasambara wa mmudzi mwa T/A Malanda Ku Chintheche mboma la Nkhata Bay. Ndili pabanja ndipo ndili ndi mwana mmodzi. +Akutulutsa chimbale chachitatu: Kasambara Mbiri ya maphunziro? Ndidaphunzira pulaimale yanga pa Lilongwe LEA pomwe ndidalemba mayeso anga a Sitandade 8, sukulu ya sekondale ndidaphunzira ku Chipasula. Ndidakapanga maphunziro a uphunzitsi ku Tanzania komwe ndidaphunzitsa kwa ka nthawi pangono ndipo padakalipano ndikupanga bizinesi. +Tatifotokozerani mbiri ya maimbidwe anu. +Ndidayamba kuimba ndili wachichepere kwambiri koma chimbale changa choyamba ndidatulutsa mu 2008 ndipo chinkatchedwa kuti Zonse ndi Yesu, chimbale chachiwiri, Nganganga ndi Yesu, chidatuluka mu 2010. Chimbale chatsopano chotchedwa Amasamala ndichikhazikitsa mu December chaka chino. +Uthenga waukulu omwe wanyamula ndi wotani? Kwakukulu uthenga omwe uli mchimbalechi ndi wa chilimbikitso kwa Akhristu anzanga mnyengo zili zonse zomwe iwo akudutsamo. +Yesu amasamala anthu ake ndipo tikamudalira iye sitidzakhumudwa chifukwa chisomo chake ndi chokwanira. +Kodi mfundo za nyimbo zimenezi mumazitenga kuti? Nyimbo zanga kwambiri zimachokera pa maulaliki a kutchalitchi komanso ndikamawerenga Baibulo ngakhalenso nthawi zina zinthu zomwe ndikuona ndi kukumana nazo. +Ndi zinthu ziti zomwe mungakonde kuti zisinthe kumbali ya zoimba mMalawi muno? Mmalo ojambulira nyimbo mwathu mukufunika zipangizo zojambulira nyimbo za mphamvu, ngati mmene kulili ku maiko a anzathu monga ku South Africa, chifukwa nyimbo zimamveka bwino kwambiri. +Phindu Mukulipeza mukuimbaku? Mmbuyomu zinthu zimavuta koma pakali pano ndi chimbale chatsopanoch tsogolo lopindula likuoneka. +Alimbana ndi ntchemberezandonda ku Zomba Unduna wa zamalimidwe wati ntchemberezandonda zomwe zabuka mboma la Zomba zisatayitse anthu mtima chifukwa akatswiri apita kale mmadera omwe akhudzidwa ndi mbozizo. +Mbozizo zapezeka kale mmadera ena mboma la Zomba mkulu wa zaulimi kumeneko Patterson Kandoje watsimikiza koma mneneri wa unduna wazamalimidwe Hamilton Chimala adati gulu la akatswiriwo likafikanso mmadera achigwa cha Shire. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Padakalipano nduna ndi gulu la akatswiri ali kale kalikiliki kulimbana ndi mbozizo ndipo iwo ndi amene angakhale ndi zonena zambiri pammene zinthu zilili, adatero Chimala. +Ntchemberezandonda zimaononga masamba ofunika pokonza chakudya cha mbewu Nduna ya zamalimidwe Dr Allan Chiyembekeza adatsimikiza kuti iye pamodzi ndi akatswiri ali kalikiliki kulimbana ndi vutoli koma adati padakalipano sanganene kuti vutolo ndi lalikulu motani popeza akadali mkati mofufuza. +Anthu angokhala ndi chikhulupiliro chifukwa akatswiri omwe akugwira ntchitoyo ndiwodziwa kwambiri moti ali ndi chikhulupiliro kuti vutoli silipita patali lisadagonjetsedwe, adatero Chiyembekeza. +Ndunayo idati chongodandaulitsa chakuti mbozizo zimaononga kwambiri panthawi yochepa komanso vuto lake ndilakuti zimadya masamba omwe mbewu zimadalira popanga chakudya motero kakulidwe ka mbewu kamasokonekera. +Ntizilombo tachabe kwambiri chifukwa timaononga masamba a mbewu choncho kuchedwa kutigonjetsa kukhoza kukhala ndi zotsatira zowawa kwambiri, adatero Chiyembekeza. +Kandoje adati pamalo okwana mahekitala 34 omwe akhudzidwa, mahekitala 6 ndiwo adali atapoperedwa pofika Lachiwiri ndipo adapempha anthu kuti akhale tcheru kuti akangoona mbozi zobiriwira zokhala ndi mizere yoyera akauze a zaulimi chifukwa maonekedwe a ntchemberezandonda ndi wotero. +Chiyembekeza: Tikuthana nazo Madera ozungulira malo a zaulimi a Mpokwa kwa T/A Mwambo makamaka midzi ya Saiti, Masambuka, Kwaitana, Mamphanda, Kabwere, Kumpatsa, Havala, Mlomwa ndi Chaima ndi ena mwa midzi yomwe yakhudzidwa. +Ntchemberezandondazi zabuka panthawi yomwe alimi akudandaula kale ndi ngamba yomwe ikutha pafupifupi sabata zitatu tsopano ndipo mbewu zambiri zanyala kale mminda moti pali chiyembekezo choti ngambayi itati yapitirira ndiye kuti alimi akhoza kudzabzalanso. +Ngambayo yadza kaamba ka mphepo ya El Nino yomwe yasokoneza magwedwe a mvula makamaka mmaiko a kummwera kwa Africa zomwe zapangitsa madera a mchigawo cha kummwera kwa Malawi akhudzidwe kwambiri. +Dansi ndi Platinum Selector Kuphunzira ndi chinthu chokoma ndipo ukasakaniza ndi luso lina la manja kukomako kumankira patali. Achinyamata ambiri omwe akuchita bwino ndi kutchuka masiku ano amadalira ntchito zamanja ngakhale sukulu adapita nayo patali. Mmodzi mwa achinyamata oterewa ndi Christopher Nhlane yemwe amadziwika ndi dzina lakuti Platinum Selector yemwe amamveka pa wailesi ya MIJ. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye pa zomwe iye amachita ku wayilesiyi Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidziwane wawa. +Ndine mwana wa nambala 5 mbanja la ana 7 anyamata atatu ndipo asungwana anayi. Ndimachokera mbomala Mzimba koma makolo anga amakhala ku Mzuzu. Ndili ndi digiri ya Business Communication yomwe ndidatengera kusukulu ya ukachenjede ya Polytechnic. +Nhlane: Zidayambira kusukulu Padakalipano umachita chiyani? Ndimagwira ntchito ku wailesi ya MIJ ngati mtolankhani, muulutsi, mkonzi ndipo nthawi zina ndimapanga mapulogalamu apadera a nyimbo chifukwa kusakaniza nyimbo ndi limodzi mwa maluso omwe ndili nawo. +Anthu amakutcha Platinum Selector chifukwa chiyani? Dzina limeneli ndidaliyambitsa ndekha kalekale mu 2010 nditayamba kuulutsa pulogalamu ya Reggae Uptown pawailesi ya MIJ FM. Ndidasankha dzinali polingalira kuti Platinum ndi chitsulo chofewa koma chopirira dzimbiri ndiye inenso pulogalamu yanga siyifwifwa ayi ndimayesetsa kuti ngakhale nyimbo zitakhala zakale koma zimamveka ngati zaimbidwa kumene kutanthauza kuti dzimbiri palibe. +Udayamba liti ndipo udayamba bwanji? Ndidayamba mchaka cha 2003 ndili pasukulu ya sekondale ya Phwezi. Nthawi imeneyo ndidali ndi chidwi kwambiri ndi akatswiri osakaniza nyimbo monga DJ Banton yemwe panthawiyo ankagwira ntchito ku wailesi ya FM 101. +Ankakuthandiza ndani? Zonse ndinkapanga ndekha ndikafatsa. Ndidali ndi kompyuta yomwe ndidalowetsamo pulogalamu yosakanizira nyimbo ndipo ndimati ndikafatsa ndimakhalira kuyeserera kusakaniza nyimbo mpaka ndidayamba kudzimva kuti tsiku lina ndidzakhala dolo. +Munthu yemwe ukakhala sufuna kumuiwala pa luso lako ndi ndani? Munthu ameneyo ndi Phil Touch yemwe ankandilimbikitsa tikugwira ntchito limodzi ku wayilesi ya MIJ. Adali munthu mmodzi yemwe adasonyeza kuti adali ndi mtima oti ine ndidzakhale dolo osalingalira zoti kaya ndidzamuposa kapena ayi, iye kwake kudali kuwonetsetsa kuti ine ndidziwe basi. +Iweyo wagwirako ntchito mmalo ati? Ndidagwirako ku Malawi News Agency (Mana) kuyambira mchaka cha 2006 mpaka 2007 kenako mchaka cha 2010 ndidalowa ntchito ku MIJ komwe ndili mpaka pano. +Akupha makwacha ndi zipatso Chaima Banda, mlimi wa zipatso kwa Manondo, T/A Nkukula ku Lilongwe, akusimba lokoma ndi ulimi wake womwe wakhala akuchita kwa zaka 10 tsopano ndipo akuti kudzera muulimiwu iye wamanga nyumba yamakono, wagula galimoto ndi kuphunzitsa ana ake msukulu zapamwamba. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Chaima, yemwe adayamba ulimiwu ngati bizinesi ya nazale za mitengo ya zipatso zosiyanasiyana akuti tsopano ali ndi makasitomala ambiri omwe amadzagula zipatso ndi mbande za mitengo kumunda wake. +Adatswirika pa ulimi wa zipatso: Banda Mlimiyu adali ngati mlimi wina aliyense wongoyeserera koma kenako adakachita maphunziro a ulimi wa bizinesi ndi momwe angalimire zipatso kuti azipindula pantchito yomwe amagwira chaka chathunthu. +Poyamba ndinkachita ulimi monga momwe amachitira alimi anzanga ndipo zinthu sizimasintha kwenikweni mpaka pomwe ndidakachita maphunziro a ulimi wa zipatso ngati bizinesi ya mbande ndi zipatso zenizenizo, adatero Banda. +Iye adati zipatso zomwe amalima zimakhala zochita kukwatitsa ndipo mtengo wake umakhala wabwino kuyerekeza ndi zipatso zamakolo zomwe alimi ambiri amadalira komanso zimakhala ndi nyengo yake. +Kwa chaka chathunthu Banda amakhala akusamalira mbande zokwatitsakwatitsa ndipo ikafika nyengo yadzinja akuti amapha makwacha ambiri pogulitsa mbandezo kumabungwe ndi anthu ena ofuna kubzala mitengo paokha. +Mwachitsanzo, mbande imodzi ya mtengo wa mango ndimagulitsa pamtengo wa K500 pomwe mapapaya ndi maolanje kapena malalanje ndi magwafa ndimachita K350. Chaka chino ndili ndi mbande 5 000 za mango, 3 000 mapapaya ndipo 2 000 magwafa zomwe ndayamba kale kugulitsa. +Mabungwe ndiwo amandigula kwambiri moti ena amandipatsiratu chiwerengero cha mitengo ndi mitundu yake yomwe adzafune. Apa zikutanthauza kuti ndimayamba kulima ndi kudziwa kale msika ndi ndalama zomwe ndikuyembekezera, adatero Banda. +Kudzera mu bizinesi ya ulimi wa zipatso womwewu, Banda adagula makina opopera madzi omwe amachitira mthirira nyengo yadzuwa. +Idali nyengo ya pasaka Wina adapitira ntchito yokatola zochitika pa tchuthi chokumbukira mazunzo ndi kuuka kwa Ambuye Yesu pomwe wina adapita kukapuma monga tchuthi koma mapeto ake idasanduka nyengo yoti awiriwa awone zomwe Mulungu adawakonzera. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mayamiko Seyani, yemwe panthawiyo amagwira ntchito ya utolankhani kukampani ya Nation Publications Limited (NPL) adali kalikiliki kutola zochitika zosiyanasiyana pomwe maso ake adakagwera pa Nicra Chikopa yemwe amadikira abale ake kuti akalowe mmadzi akasambire. +Mayamiko akuti atangomuona Nicra, ntchito yonse idasokonezeka ndipo sadaupeze mtima mpaka adatsatira pomwe padali namwaliyo nkuyamba kucheza naye. +Mayamiko ndi Nicra tsiku la chinkhoswe chawo Ndidali ndi anzanga pa nthawiyo koma ndidawasiya ndipo nawonso adandimvetsetsa chifukwa sinkadachitira mwina ayi koma kusendera kufupi, adatero Mayamiko. +Nicra akuti machezedwe a Mayamiko adamusangalatsa kwambiri moti adaiwala zokasambira abale ake omwe amadikira atafika. +Tidacheza ngati anthu oti tidadziwana kalekale pomwe ayi ndithu kadali koyamba moti adandipatsa chidwi kwambiri, adatero Nicra. +Chitatha tchuthi, awiriwa akuti adakumananso mumzinda wa Blantyre momwe onse amakhala ndipo macheza awo adapita patsogolo kufikira pomwe Mayamiko adamasuka lilime nkufunsira. +Zonsezi akuti zinkachitika mchaka cha 2014 ndipo kuyambira apo mpaka lero, chibwenzi chawo chakhala chikuyenda bwino moti pa 4 October chaka chomwe chino adamanga chinkhoswe kuyembekeza ukwati oyera chaka chamawachi. +Mayamiko akuti kwa iye Nicra ndi mkazi yekhayo yemwe adamutenga mtima mpaka njala ya chakudya kutha ndipo akuti salotako zoti nkudzalekana naye. +Nicra naye akuti chake nchisangalalo chokhachokha popeza mwamuna wa kukhosi kwake ndipo naye akuti alibenso nkhawa za tsogolo lowala. +Palibe yemwe amada nkhawa atapeza chinthu chomwe amalakalaka mmoyo mwake. Ine ndidapeza mwamuna yemwe ndinkalakalaka wachikondi, wachilimbikitso komanso owopa Mulungu, adatero Nicra. +Mayamiko amachoketra mmudzi mwa Nankwana kwa T/A Makwangwala mboma la Ntcheu pomwe Nicra amachokera mmudzi mwa Nguluwe, T/A Bvumbwe, Thyolo. +Mwayi kuthima kwa magetsi Pomwe ena akudandaula za kuthimathima kwa magetsi, ena akusimba lokoma kuti adapatirapo mwayi wabanja. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Victor Mpunga yemwe pa 28 December 2015 adapanga chinkhoswe ndi Mary Makhiringa, akuti adayamba kulankhulana pagolosale pomwe Mary amakagula chakudya atachita ulesi kusonkha moto magetsi atathima. +Victor ndi Mary adakumana pagolosale Victor akuti nthawi zambiri amakonda kucheza pagolosale yamnzake pafupi ndi pomwe Mary amakhala ndipo amangomezera malovu msungwanayu akamadutsa popita ndikuchokera kuntchito. +Iye akuti mwayi udapezeka tsiku lina madzulo magetsi atathima pamenepo Mary akuchokera kuntchito ndipo mmalo mosonkha moto kuti aphike nkhomaliro, adangoganiza zokagula chakudya pagolosaleyo ndipo nkuti Victor ali pomwepo. +Ndidangoti bowa bwanga nthawi yomweyo nkuyambitsa macheza. Ndimaona ngati andinyoza malinga ndi mmene amaonekera koma ayi ndithu tidacheza bwinobwino mpaka chinzake chidayamba, adatero Victor. +Iye adati chinzakecho padali polowera chabe chifukwa patangotha nthawi pangono chibwenzi chidayamba mpaka makolo kudziwitsidwa nkuyamba kupanga dongosolo la chinkhoswe. +Iye adati ulemu amamusangalatsa kwambiri chifukwa cha mawonekedwe, khalidwe ndi luntha pofuna kupanga chinthu ndipo salola kupanga chinthu chomwe sakuchimvetsetsa zomwe iye amaona ngati mphamvu. +Mary adati kwa iye chachikulu nchakuti Mulungu adamulozera mwamuna yemwe amayembekezera moti ali ndi chiyembekezo chakuti adzakhala pabanja lokoma ndi losangalatsa kwambiri. +Ndimamukonda kwambiri Victor chifukwa ndi mwamuna wachitukuko. Ndi munthu uja oti akaganiza kapena kunena chinthu amayesetsa mpaka chichitike basi ndiye ndimadziwa kuti ali nkuthekera kwakukulu, adatero Mary. +Awiriwa akuti akuyembekezera kumanga ukwati woyera chaka chino cha 2016 ndipo zokonzekera zili mkati. +Mphwiyo, Kasambara akadali mchitokosi Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Pamene bwalo la milandu ku Lilongwe likupitiriza kumva nkhani za amene akuwaganizira kuti adatengapo gawo posolola ndalama za boma, yemwe adali woyendetsa chuma cha boma Paul Mphwiyo komanso nduna yakale ya zachilungamo Ralph Kasambara akadali mchitokosi. +Akadali mkati: Mphwiyo Kasambara akuyankha mlandu womuganizira kuti adakonza chiwembu chofuna kupha Mphwiyo pamene Mphwiyo akuyankha mlandu womuganizira kuti adatengapo gawo poba K2.4 biliyoni ya boma. Iye adamangidwa Loweruka lapitalo pomwe oganiziridwa ena pamlanduwo Auzius Kazombo Mwale, Clemence Mmadzi ndi Roosevelt Ndovi adatulutsidwa pabelo Lachitatu. +Lachinayi, wachiwiri kwa mkulu wa bungwe lothana ndi ziphuphu la Anti-corruption Bureau (ACB) Reyneck Matemba yemwe amaimira boma pamlanduwo mmalo mwa mkulu wa oimira boma pamilandu Mary Kachale adapempha wogamula Esmie Chombo kuti Mphwiyo asungidwebe mchitokosi kwa sabata ziwiri. +Apolisi ofufuza za ndalama apeza maumboni ena okhudzana ndi Mphwiyo ndipo potha sabata ziwiri akhala atamaliza zofufuza zawo. Ngati adzakhale asanamalize, tidzalola kuti atuluke. Sikuti tikungofuna kumuzunza, adatero Matemba. +Mphwiyo ali ndi milandu 17 yokhudza zosololazo. +Ndipo woweluza kubwalo lalikulu la Lilongwe Rezine Mzikamanda dzana adati pofika Lachisanu sabata ya mawa, Kasambara adzakhala atadziwa ngati angatuluke kapena ayi. Izi adanena woimira Kasambara Modecai Msiska adapempha bwalolo kuti litulutse Kasambara chifukwa woweluza Michael Mtambo adabweretsa nkhani yoti Kasambara asakhalenso pabelo kukhoti yekha nkulamula kuti Kasambarayo alowenso mchitokosi. +Manja mkhosi ndi kupsa kwa misika Pamene nkhani yakupsa kwa misika yayala nthenje mdziko muno, amalonda ena achita jenkha, kusowa mtengo wogwira katundu wawo atasakazidwa ndi moto. +Chisale watuluka nkumangidwanso Escom in free-for-all fuel scam Wait gets longer Posakhalitsapa, misika ya Area 18 ku Lilongwe, wa Kasungu, Vigwagwa ku Mzuzu, Kamuzu Road ku Salima komanso wa Karonga yapsa ndipo katundu wa nkhaninkhani wasakazidwa. +Mmodzi mwa okhudzidwa ndi kuyaka kwa msika wa Vigwagwa wati akusowa mtengo wogwira pamene katundu wake wa K1.3 miliyoni adayakiratu. +Kupsa kwa misika ndiyo nkhani ili mkamwamkamwa Ndithandiza bwanji abale anga 11 omwe amadalira ine? Chopweteka kwambiri nchakuti ndidali nditangotenga ndalama kumene kukagula katunduyo, adatero Banda. +Wapampando wa komiti ya pamsika wa Vigwagwa, Gerald Maulana, adati komiti yoona za ngozi za moto yapangidwa yomwe iziona za momwe angathanirane ndi ngozizo komanso kupezeka kwa madzi ozimitsira moto azikhala pafupi. +Maulana adati anthu omwe adali ndi ngongole akuwathandiza powalembera makalata opita kukhonsolo ndi mabungwe opereka ngongole ngati umboni kuti katundu wawo adapsa. +Iye adati: Zaka za mmbuyozo anthu ankagwiritsa ntchito moto ngati njira yobela katundu koma apolisi adakhwimitsa chitetezo ndipo palibe amene adadandaula kubedwa kwa katundu pa nthawi ya moto. +Ndipo Lachitatu polankhula phungu wa pakati mboma la Kasungu Amon Nkhata atapereka simenti yokwana K1.5 miliyoni yogulira matumba 200 a simenti kuti msika wa Kasungu umangidwenso, wapampando wa mavenda mumsikawo Burnet Saudi adati padakalipano manja awo ali mkhosi. +Tikupempha akufuna kwabwino ena athandize mnjira zosiyanasiyana chifukwa mavuto ndiye ngambiri, adatero iye. +Padakalipano, mneneri wapolisi mdziko muno Rhoda Manjolo wati apolisi amayamba afufuza kaye asanamange munthu. Mawuwa adadza pamene mneneri wa unduna wa maboma aangono Muhlabase Mughogho adati kusamangidwa kwa anthu ootcha misika ndiko kukuchititsa mchitidwewu kuti ukule. +Mughogho adati palibe chasintha pa mfundo za chikalata chimene undunawo udatulutsa chaka chatha. +Malinga ndi chikalata cha chaka chathacho, makhonsolo ayenera kukhala ndi zozimira moto zokwanira mmisika kuti ngozi itagwa asasowe mtengo wogwira. +Minibasi zivuta pa Wenela Si kuti ndikamba za kutentha kwa pa Wenela. Si kuti ndinena za kukwera mtengo kwa zinthu. Si kuti ndinena za chipasupasu chagundikanso ku Ukafuna Dilu Fatsa. Ayi, sindinena zonsezo. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Si kuti ndibwereza kunena nkhani ya othawa nkhondo uja Adona Hilida. Pajatu wamisala adaona nkhondo, ngakhale adali kulota chabe. +Inde, ngati mumayembekezera kuti ndinena za amisala ena amene akunena zamisala kuti kusiyana pakati pa osauka ndi olemela kusakhale kwakukulu mwalemba mmadzi. Abale anzanga, izi zingatheke pa Wenela pano? Zingatheke bwanji osauka ndi olemera kukhala osasiyana kwambiri? Zingatheke bwanji pamene ana a anthu olemera akuphunzira sukulu zodula pomwe ana a amphawi akuphunzira pansi pa mtengo ngakhale mvula ikugwa? Sindinenanso kuti nzosatheka, zili ngati ngamira kuyesera kulowa pabowo la singano. Zitheka bwanji pomwe osauka akupatsidwa Panado pomwe akudwala malungo chonsecho olemera olamula ndi otsutsa akutumiza ana awo kuzipatala za ku Soweto? Misala! Zosatheka! Za ziiii! Zopanda ndi kamchere olo kamodzi! Pa Wenela tsikulo padavuta. Kudali chifwirimbwiti. Nkhani idavuta ndi ya minibasi. Nthawiyo nkuti apolisi atagwira minibasi zosachepera 70. +Chifukwa? Ati timatenga mafolofolo. Kodi okwera timawakakamiza kukwera folofolo? Ndimayesa iwowo amapanikizana ngati nsomba zamchitini chifukwa amakhala pachangu? Kodi okwera sadziwa kuti tikaloza chala pansi ndiye kuti tikufunsa ngati kutsogolo kuli boma? Kodi sadziwa kuti tikazindikira kuti kuli boma, mmodzi kapena awiri amene anachititsa kuti ilakwe atsika? Kodi iwowo sadziwa kuti ngati yalakwa ndi mmodzi kondakitala akhoza kutsika nkuuza mzibambo mmodzi agwire chitseko ngati kondakitala, iye nkuthamanga kudutsa boma? Simudaonepo woyendetsa akuuza wokwera mpando wakutsogolo kuti akhalire lamba poopa boma? Mudaona wokwerayo akukana? Ndiye kudali kuotcha mateyala. +Mutibwezere mabasi athu! Mugwira bwanji mabasi, mukufuna tikadye kuti? adali kuimba chotero makondakitala, madalaivala, ife oitanira komanso ena okwera. +Chitamponi kanthu pa za fisp Wapampando wa komiti ya zaulimi mNyumba ya Malamulo, Felix Jumbe, wati boma lichitepo kanthu pa za mmene ndondomeko ya Farm Input Subsidy Programme (Fisp) ya zipangizo zaulimi zotsika mtengo ikuyendera polingalira kuti nthawi ikutha. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Jumbe adalankhula izi pocheza ndi Uchikumbe potsatira lipoti la pa 5 January la mmene ntchitoyi ikuyendera lomwe likusonyeza kuti kufika pano, pamatumba 100 alionse a feteleza, 76 okha ndiwo adafika kumalo ogulitsirako zipangizozi. +Ngakhale ena agula kale zipangizo, madera ena sizidafike Malingana ndi Jumbe, iyi ndi nkhani yoopsa chifukwa mbewu zimakhala ndi nyengo yake yomwe zimachita bwino zikalandira feteleza ndipo kuti kuthira feteleza nyengoyi itadutsa kale sikungapindule kanthu kwa mlimi. +Fetelezatu sangothirapo poti wapezeka ayi. Pali nyengo yake malingana ndi mmene mbewu zikukulira chifukwa zikadutsa pena pake, kuthira feteleza kumangokhala kuononga chabe. +Mwachitsanzo, munthu ungamathire feteleza wokulitsa chimanga chitayamba kale ngaiyaye nkumati ukuchitapo kanthu? Mwezi wa January alimi amayenera zipangizo ali nazo pafupi, adatero Jumbe. +Nyuzipepala ya The Nation ya pa 8 January idasindikiza kuti zotsatira za mkhumano wa pakati pa nduna ya zamalimidwe, ulimi wamthirira ndi chitukuko cha madzi, Allan Chiyembekeza, ndi eni makampani omwe zikunyamula zipangizozi, adagwirizana kuti ntchitoyi ikuyenera kutha pofika pa 31 December, 2015. +Malingana ndi Jumbe, pomafika pa 5 January ntchitoyi inali ikadali mkati zikusonyeza kuti pena pake pali vuto mndondomekoyi ndipo mpofunika kuti akuluakulu omwe akuyendetsa ntchitoyi achitepo kanthu msanga. +Nduna ya zachuma ndi chitukuko, Goodall Gondwe, adauza nyuzipepala yomweyi kuti anthu akupupuluma kufalitsa zolakwika za pulogalamuyi zomwe zikusemphana ndi momwe ikuyendetsedwera chaka chino. +Iye adati nzomvetsa chisoni kuti zaka zingapo chiyambireni pulogalamuyi, anthu ena amaganizabe kuti idayambitsidwa ndi cholinga chothetsa umphawi pomwe cholinga chake nchakuti anthu azikhala ndi chakudya chokwanira. +Cholinga cha pulogalamuyi nchakuti anthu azikolola chakudya chokwanira koma anthu ena amaganiza kuti idabwera kudzathetsa umphawi. Maganizo otere ndiwo amachititsa kuti anthu aziyembekeza kuthandizidwa chaka ndi chaka, adatero Gongwe. +Mabungwe athotha galu wakuda ku MJ Anthu mboma la Mulanje omwe adakhudzidwa ndi njala kaamba ka ngozi za kusefukira kwa madzi komanso chilala kumayambiriro a chaka chino akuombera kuphazi mabungwe angapo atamva pempho lawo la kufunika kwa chakudya kuti apulumutse miyoyo yawo ku njala. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mabungwe a Oxfam, Save the Children, Goal Malawi, Concern Universal, Irish Aid ndi ena ndiwo adachita chamuna posonkha ndalama zoposa K7 biliyoni zomwe zathandiza kuti galu wakuda yemwe adadutsa mbomali ayambe kuona msana wa njira. +Gogo kutsekulitsa akaunthi ya Airtel Money Mwambo wokhazikitsa chithandizochi udachitika ku Mulanje sabata yatha pamene akuluakulu a mabungwewa komanso mafumu adachitira umboni kuyamba kwa ntchito yothandiza anthu ovutika ndi njalawa. +Kazembe wa dziko la Norway ku Malawi, Kikkan Haugen, adati pofuna kuonetsetsa kuti palibe chinyengo pa ndondomeko yothandiza anthuwa, mgwirizano wawo wasankha kampani ya foni zammanja ya Airtel kuti anthu azilandira chithandizo cha ndalama zogulira chimanga, mafuta ophikira ndi nyemba kapena nandolo kudzera ku kampaniyi. +Wogwirizira udindo wa mkulu wa kampani ya Airtel, Charles Kamoto, adati kampani yawo ithandizira ndondomekoyi kudzera mu Airtel Money. +Chomwe chizichitika nchakuti mwezi uliwonse munthu aliyense [amene ali pamndandanda wolandira nawo thandizoli] azilandira K15 800 yoti agulire thumba limodzi la chimanga, malita awiri a mafuta ophikira ndi nyemba kapena nandolo zolemera makilogalamu 10. +Ndiye chomwe tapanga nchoti aliyense tamutsekulira akaunti ya Airtel Money yomwe azilandirirako ndalamayo. Ndipo zikalowa atha kupita kwa maejenti anthu amene ali mboma lomwelino kukatenga ndalamazo zokagulira chakudya, adatero Kamoto. +Malinga ndi Haugen, ndalamazi zizitumizidwa mwezi uliwonse kuti anthu asatuwe ndi njala. +Olandira makuponi pano mu 2016 sadzalandiranso Boma lati kuyambira chaka chino, yemwe wapindula nawo mupologalamu ya zipangizo zaulimi zotsika mtengo ya Farm Input Subsidy Programme (Fisp) wadyapo gawo lake lotsiriza chifukwa chaka chamawa kunka mtsogolo Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu sadzapezekanso pamndandanda wa olandira makuponi. +Nduna ya zamalimidwe, ulimi wamthirira ndi chitukuko cha madzi, Allan Chiyembekeza, ndiye adalengeza izi pamsonkhano wa atolankhani kulikulu la undunawu mu mzinda wa Lilongwe Lachiwiri lapitali. +Iye adati boma lachita izi poona kuti anthu omwe amapindula mupologalamuyi ndi omweomwewo koma saonetsa kusintha kulikonse, zomwe zidachititsa maiko ndi nthambi zomwe zimathandizirapo mpologalamuyi kugwa mphwayi. +Mwayi womaliza: Ogula feteleza ndi mbewu za sabuside chaka cha mawa adzadzigulira okha Pologalamuyi idayambitsidwa ndi cholinga chopatsa alimi poyambira kuti zikawayendera azidzidalira koma malipoti akusonyeza kuti anthu omweomwewo ndiwo amalandira makuponi chaka nchaka popanda kuonetsa kusintha kulikonse, adatero Chiyembekeza. +Iye adati poona izi, boma laganiza kuti lipereke mwayi umodziumodzi kwa anthu oyenera thandizoli ndipo yemwe zimukanike azidzionera yekha zochita mtsogolo chifukwa mwayi upita kwa anthu ena. +Pakalipano, tili ndi mndandanda wa alimi a chimanga okwana 4.2 miliyoni ndipo mwa amenewa, tasankhamo alimi 1.5 miliyoni omwe athandizike chaka chino koma asayembekezere kuti chaka chamawa adzapezekanso pamndandanda wa alimi olandira makuponi, adatero Chiyembekeza. +Koma wapampando wa komiti ya zaulimi mNyumba ya Malamulo, Felix Jumbe, sakugwirizana ndi ganizoli ponena kuti kumeneku kukhala kuweta umphawi wadzawoneni mdziko muno. +Potsirapo ndemanga pa zomwe Chiyembekeza adanena, Jumbe adati nzosatheka anthu ovutikitsitsa kusintha nkukhala odzidalira paokha chifukwa cha matumba awiri a feteleza ndi paketi imodzi ya mbewu chifukwa zosowa pamoyo ndi zambiri. +Zimenezi nkungofuna kunyeketsa Amalawi opsa kalewa. Zoona munthu angasinthe ndi matumba awiri a feteleza ndi paketi imodzi ya mbewu basi? Ngati akufuna apange ndondomeko yabwino adzapereke zipangizo zokwanira zoti mlimi akhozadi kuimirapo iwo akasiya kupereka thandizo, adatero Jumbe. +Iye adati mmaiko ena monga Zambia, alimi ena adakwanitsa kuima paokha chifukwa boma lidawapatsa zipangizo zokwanira-matumba 8 mlimi mmodzi-moti pano adaleka kudalira boma. +Jumbe adati njira yomwe boma la Malawi limatsata mupologalamu ya sabuside ndi yongopeputsa alimi osati kutukula ulimi monga momwe maiko otukuka adachitira kwawo. +Naye mfumu yaikulu Kabudula ya ku Lilongwe idadandaula ndi ndondomekoyi yatsopanoyi ponena kuti zikakhala choncho ndiye kuti anthu ambiri azivutika ndi njala komanso umphawi. +Alimi ambiri malo awo olima ndi ochepa kwambiri moti ngakhale akolole nkugulitsa zonse sangadzakwanitsebe kugula feteleza ndi mmene udakwerera mtengomu. Thumba limodzi la feteleza ndi K23 000 pomwe la chimanga ndi K5 000 kutanthauza kuti mlimi akuyenera kusunga matumba 5 a chimanga kuti adzagule thumba limodzi la feteleza. +Nanga poti alimi ambiri amafuna matumba a feteleza 4 kapena kuposa apo ndiye kuti agulitse matumba angati a chimanga kuti aime paokha? Mwinanso pakhomopo pali ana angapo akufunika fizi, zovala ndi kudya, adatero Kabudula. +Mwezi wathawu, akadaulo pankhani za kayendetsedwe ka chuma a Economics Association of Malawi (Ecama) adalangiza boma kuti pologalamu ya sabuside ikuyenera kutha kaamba koti imapsinja ndondomeko ya chuma (bajeti). +Ngakhale mmadera ambiri mvula yobzalira yagwa kale, katundu wa sabuside yemwe wafika kale mmisika yomwe idakhazikitsidwa kuti anthu azikagulira zipangizozi sakukwana theka la katundu yense yemwe akufunika mupologalamuyi. +Mu pologalamu ya chaka chino, boma lakonza feteleza wokwana matani 150 000 omwe yemwe agawidwe pakatimpakati wokulitsira ndi wobereketsera ndipo matani okwana 3 000 ndi a mbewu za mtundu wa nyemba, soya, khobwe, nandolo ndi mtedza. +China chomwe chasintha mu pologalmu ya chaka chino ndi mitengo yomwe alimi azigulira zipangizozi monga K3 500 thumba la fetereza, K1 500 mbewu yachimanga ndinso K500 mbewu za mtundu wa nyemba. +Mitengoyi ndiyokwererapo kuyerekeza ndi mitengo yammbuyomu ati pofuna kuchepetsa ndalama zomwe boma limaononga mupologalamuyi. +Nduna ya zachuma Goodall Gondwe adati boma limaononga ndalama zankhaninkhani mupologalamuyi motero lidaona kuti nkoyenera kuwonjezera ndalama yomwe alimi amaikapo mupologalamuyi. +Kunalibe kubera mu 2015Maneb Wapampando wa bungwe loona za mayeso la Malawi National Examinations Board (Maneb) John Saka wati bungweli ndi lokondwa kuti mchaka cha 2015 mayeso onse amene bungweli limayendetsa adayenda bwino chifukwa padalibe zobera. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Polankhula kwa atolankhani ku Sunbird Mount Soche mumzinda wa Blantyre Lachiwiri, Saka adati ali ndi chikhulupiriro chonse kuti bungweli lathetsa kubera mayeso. +Akuti zobera mayeso zikuchepa Iye adati pamayeso onse atatu a Primary School Leaving Certificate of Education (PSLCE), Junior Certificate of Education (JCE) ndi Malawi School Certificate of Education( MSCE) lidakumana ndi vuto limodzi lokha lokhudza kubera mayeso pa JCE. +Saka adati: Iyi ndi nkhani yosangalatsa kwambiri poyanganira momwe zakhala zilili pankhani yobera mayeso mdziko muno zaka zingapo zapitazo. +Ndife okondwa kuuza dziko lonse kuti mayeso a mchaka cha 2015 ayenda bwino kwambiri ndipo sanabedwe. Zotsatira zimene zidatuluka ndi zoona zenizeni za mmene ophunzira aliyense adalembera mayeso ake. Tipitiriza kuonetsetsa kuti mayeso asadzabedwenso. +Wapampandoyo adati izi zidatheka chifukwa cha mgiwrizano umene ulipo pakati pa magulu osiyanasiyana amene amatengapo mbali poyendetsa ntchito za mayeso mdziko muno monga apolisi, asilikali a nkhondo, aphunzitsi, boma ndi ena onse. Iye adaonjezera kuti chitetezo cha mapepala amayeso chakwera kwambiri chifukwa cha njira yatsopano imene idakhazikitsidwa mchitidwe wobera mayeso utafika poipa. +Anatchezera Mayi anga amandilodza Anatche, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Zikomo gogo chifukwa cha malangizo amene mumapereka kwa ife awerengi anu. Anga ndi mantha pa zomwe amandichita mayi anga. +Anzawo kwambiri adandiuzapo kuti mayiwo adandiikira mankhwala mchakudya kuti ndisiyane ndi mkazi wanga. Malinga ndi zochitika pakhomo pathu, sindikudabwa nazo izi. +Ndimapezeka kuti ndikumuchitira nkhanza zosadziwika bwino mkazi wanga ngakhalenso ana athu. Ndipo nthawi zina ndimamuuziratu kuti achoke pakhomopo pa zifukwa za ziii! Pena ndikakhala bwino, ndimamukonda mkaziyo koma zikangogundika kumakhala ndewu osati masewera. Ankhoswe adasiya kubwera kudzagamula nkhani zathu. Nanenso ndatopa nawo moyowu. +Ndichitenji? LW, Blantyre. +LW, Nkhani yanu ndi yomvetsa chisoni. Zakuti ena amatha kuchitira zoipa zotere ana awo ndimadziwa. Ena amatha kuchitira mankhwala ana awo kuti asaadzakwatire kapena kuti aziwakonda kwambiri. +Ndine mmodzi mwa amene amakhulupirira kuti padziko lapansi pali ochita zabwino ndi ochita zoipa. Mayi anu akhoza kukhala ndi mphamvu yochita zoipa. +Langizo langa kwa inu ndi lakuti, mulimbikire kupemphera kuti chiwanda chili ndi mayi anu chisakukhudzeni. Pofika pokhala ndi ana awiri si masewera ndiye izi zikhoza kungokusokonezani zitukuko za pakhomo panu. +Langizo langa lalikulu ndi lakuti, musayerekeze kupita kwa asinganga chifukwa kumeneko mukangopusitsidwa chabe. Akhoza kukufunsani mafunso inu kumuonetseratu mukukaikira mayi anu kuti akukulodzani. Nanga akakakuuzani kuti muwakonze? Adandithawa Gogo wanga, Ndinali paubwenzi ndi msungwana wina wa ku Nkhata Bay kwa chaka. Mwadzidzidzi, iye anathetsa chibwenzicho pa zifukwa zosadziwika bwino. Koma ndakhala ndikumuthandiza pa maphunziro. Ndidapeza chibwenzi china ndiye akubwera ati tibwererane. +FG, Machinga. +FG, Ameneyotu amafuna kukutayani chifukwa anaona mawanga ena. Mwinatu anali ndi chikhulupiriro kuti apeza mwamuna wina, kapena alipo wina amamunamiza. Mwina kumenekonso zakavuta kapena mwamunayo wamutaya. +Musakhale naye ntchito ameneyo, si mwati ichi nchibwenzi? Chibwenzitu ndi njira yodziwira munthu amene ungadzamange naye banja ndiye ngati uyu akukutayani popanda chifukwa chenicheni musanalowe mbanja mutayeni angadzakuvuteni kutsogoloku. +Muyeneranso kuzindikira kuti kunjaku kwaopsa. Ino si nthawi yomangosinthana akazi ngati zovala. +Apongozi, alamu ovuta Anatchereza, Ndine mnyamata wa zaka 23 ndipo ndili ndi mwana wa mwamuna wa chaka chimodzi. Ndimagwira ntchito ku Lilongwe. Vuto lalikulu ndi apongozi anga komanso abale a mkaziyo. Iwo amachita zonse zotheka kuti ndisiyane ndi mkazi wanga. Ndichitenji? BB, Lilongwe. +BB, Nkhani yanu ndiyovuta kuyankha chifukwa mwangobenthula pangono. Kodi iwowo amati vuto ndi chiyani? Kodi mkazi wanuyo mudatengana naye bwanji? Ukwati wanu ulibe ankoswe? Kodi mukukhala pachitengwa? Nzovuta kukuthandizani chifukwa simunatambasule bwino nkhani yanu. Zikomo. +Ofuna mabanja Awerengi, ndisanakupatsireni mndandanda wa ofuna mabanja amene atumiza mauthenga awo sabata ino, ndati ndinenepo nkhani imene yakhala ikundikhudza makamaka patsamba lino. +Ndimalandira mauthenga ambiri a achinyamata amene amanena kuti akufuna mayi wamkulu kuposa iwo. Ambiri mwa achinyamatawa amati akufuna mayi wakuti ali ndi chuma kale. +Monga gogo, izi zimandikhudza. Mauthengawa ndikamaika sikuti zimandisangalatsa koma chifukwa monga gogo ndimalemekeza ufulu wa wina aliyense kupeza wachikondi wake. Uthenga umene sitiika ndi umene ndaona kuti ukukhudza ana. +Tsono langizo langa kwa anyamata amene amafuna mkazi wamkulu, wachuma kale ndi lakuti, uwu ndi ulesi waukulu. Nchifukwa chiyani mukufuna kupeza yophaipha? Chuma simungachipeze kupyolera mkukwatira wa chuma kale. Ichi nchimasomaso. Dekhani komanso dzilimbikireni nokha. Mukadzakhala pabwino, simudzavutika kupeza kazi wa kukonda kwanu. +Abambo odzikhweza akuchuluka Kafukufuku wa apolisi mdziko muno waonetsa kuti abambo 90 ndiwo amadzipha pa anthu 100 alionse amene amatenga miyoyo yawo podzikhweza kapena kudzipha mnjira zina. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Malinga ndi mneneri kulikulu la polisi, Nicholas Gondwa, abambo ambiri amalimba mtima ndi kudzipha kusiyana ndi amayi. +Koma amayi ndi olimba mtima, amakumana ndi nkhanza zambiri, koma ndi ochepa omwe amadzichotsera moyo, iye adatero pocheza ndi Msangulutso. +Polankhulapo, mneneri wa apolisi mchigawo cha kumpoto, Maurice Chapola, adati abambo ambiri akakumana ndi nkhaza za mbanja amathamangira kudzipha mmalo mokadandaula kunthambi ya polisi ya Victim Support Unit (VSU). +Chapola adati abambo khumi ndiwo amakadandaula ku VSU mwa anthu 100 alionse. +Kondwani Machano yemwe ndi bambo wa ana awiri, adati abambo amaopa kupita kupolisi akakhala ndi nkhawa kuopa kuukiridwa komanso chifukwa ambiri mwa iwo sadziwa kulankhula. +Ndipo katswiri woona zakaganizidwe (psychiatrist), yemwenso ndi mkulu wa chipatala cha St John of God mmzinda wa Mzuzu, Charles Masulani Mwale, adati abambo ambiri akakhala ndi mavuto a mmaganizo, sagawira anzawo za nkhawazo kuopa kuoneka opusa. +Abambo amaopa kuoneka opepera akauza ena za mavuto awo ndipo amawasunga mmaganizo, pomwe amayi amagawana nkhawa zawo, Masulani adatero. +Iye adati abambowa amakakamira kuthana nawo okha mavuto omwe ali nawo. +Masulani adati kafukufuku waonetsa kuti ngakhale amayi ambiri ndiwo amalingalira zodzipha, ambiri mwa iwo sadzipha kaamba koti amatsatira njira zozizira zodziphera pomwe abambo omwe amalingalira zodzipha amagwiritsa ntchito njira zoopsa pochotsa miyoyo yawo. +Tinene kuti amayi amangoopseza kuti adzipha kusiyana ndi abambo omwe akalingalira, amachotsadi moyo wawo mnjira zoopsa, Masulani adatero. +Iye adati vuto lodzipha ndi lalikulu mmaiko otukuka kumene ati kaamba koti anthu sadziwa kopita akakhala ndi mavuto a mmaganizo. +Sitidazolowere kuti tikakhala ndi nthenthe kapena kupanikizika mmaganizo tiyenera kupita nazo kuchipatala, koma izi zimafunika thandizo lamsanga la akatswiri odziwa za kaganizidwe, Masulani adatero. +Iye adati pachipatala cha St John of God amayi ambiri ndiwo amafuna thandizo kusiyana ndi abambo. +Masulani adati ambiri mwa amayiwa amavutika mmaganizo chifukwa cha mavuto a mbanja komanso umphawi. +Ambiri amati mwina angodzipha chifukwa umphawi wafika povuta ndipo chilichonse chomwe ayesa sichikuyenda, Masulani adatero. +Alimi musaiwale mitengo ya chonde Bungwe lomwe limalimbikitsa alimi kubzala mitengo yosiyanasiyana la World Agroforesry Centre lapempha alimi kuti asaiwale mitengo ya chonde akamabzala mitengo chaka chino. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Woyendetsa pologalamu ya Agroforestry Food Security yomwe cholinga chake nkuonetsetsa kuti alimi akukhala ndi chakudya chokwanira, Dr Bruce Sosola, adati kugwiritsa ntchito mitengo ya chonde kukhoza kuchulukitsa zokolola ndi katatu pamunda. +Mkuluyu adalankhula izi pomwe amayendera nazale za mitengo za alimi ku Lumbadzi Lachiwiri lapitali komwe adati ndi wokhutira ndi ntchito yomwe alimi akuchita pankhani yobwezeretsa chilengedwe. +Sosola adati ina mwa mitengoyi monga Gliricidia ikhoza kugwiritsidwa ntchito limodzi ndi mbewu monga chimanga pomwe ina imafuna kuibzala mwakasinthasintha ndi mbewu ndipo imatha kugwiritsidwa ntchito kwa zaka ziwiri kapena zitatu mlimi asanabzalenso ina. +Sosola kuyendera nazale ya mitengo yobwezeretsa chonde mnthaka Kafukufuku yemwe tidapanga mmbuyomu adasonyeza kuti alimi akhoza kupindula kwambiri ndi njirayi chifukwa amalowetsa ndalama zochepa muulimi wawo. Pali mitengo ina monga ya Gliricidia yomwe mlimi akhoza kuphatikiza ndi mbewu monga chimanga popanda kusokoneza kakulidweka chimangacho. +Mitengoyi imathandiza kubwezeretsa michere yachilengedwe mnthaka. Komanso imagwira bwino kwa mlimi yemwe ali ndi malo ochepa chifukwa amabwezeretsa chonde mnthaka pomweso akulima mbewu zake nthawi imodzi, adatero Sosola. +Iye adati ubwino wina wa mitengoyi ndi wakuti imayamwa mchere wa Nitrogen ndi kuwusunga mmasamba ake ndi kuyamwanso mchere wachilengedwe womwe udathawira pansi ndi madzi nkuwubweretsa pamwamba kuti mbewu zizigwiritsa ntchito. +Kupatula Gliricidia, Sosola adati paliso mitengo ina monga katupe (Tephrosia), Sesbania, Cajanus komanso Faidherbia yomwenso imagwira ntchito yobwezeretsa chonde munthaka. +Iye adati mbewu yamitengoyi ndi yosavuta kupeza ndipo alimi akhoza kuipeza kudzera kumaofesi a bungweli omwe ali ku Chitedze Research Station ku Lilongwe pamtengo wotsika. +Iye adati bungweli limapereka upangiri kwa alimi omwe ali ndi chidwi chotsata njirayi momwe angachitire kuti apeze phindu lochuluka. +Adatinso ena mwa alimi omwe adawaphunzitsa kale pano adasanduka odziyimira paonkha ndipo akumagwiranso ntchito yophunzitsa alimi anzawo. +Mayi Dorothy Themba wochokera kwa Mpingu ku Lilongwe adathirira umboni kuti banja lawo lapindula kwambiri ndi njirayi. Iwo adati tsopano akukolola pafupifupi milingo itatu pa mbewu zomwe amabzala kuyerekeza ndi zomwe amakolola poyamba pamunda womwewo. +Ndidazindikira mochedwa kuti njirayi ndi yopindulitsa kwambiri. Mchaka choyamba kugwiritsa ntchito njirayi zokolola zanga zidawonjezekera koma apa nkuti mitengoyi isanayambe kugwira ntchitokwenikweni. +Apumphuntha ana ndi nsimbi Ana atatu a banja limodzi abwerera lokumbakumba mayi wawo Eveter Kulemera, wa zaka 24, akuti atawalumira mano kuwapumphuntha ndi nsimbi yotchezera mowa wa kachasu mmudzi mwa Pemba kwa T/A Kachere mboma la Dedza. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Pakalipano mwana mmodzi, wa zaka ziwiri, ali chigonere mutu uli chitupile mchipatala cha boma cha Dedza pomwe mbale wake, wa zaka zitatu, akuvutika ndi msana ndipo wina wa zaka zisanu ali nkhasako chifukwa akuti adakwanitsa kuthawa ataona zomwe makeyo amachita. +Gogo wa ana ndi mchemwali wa mayi yemwe adavulaza ana ake kudwazika matenda mchipatala cha Dedza Lachinayi Gogo wa anawo Catherine Moses, yemwe akudwazika matendawo, adati pa 17 December, khunyu lidagwira mayi wa anawo dzuwa likuswa mtengo ndipo atatsitsimuka adatenga mankhwala onse omwe adalandira kuchipatala nkumwa ati kuti afe. +Iye adati pambuyo pake adayamba kutukwana anthu pamudzipo uku akunena kuti akufuna afe koma atenga ana ake ngati mitsamiro, koma anthu amaona ngati tchetera poti nthawi zambiri amatero nthendayo ikayamba. +Poyamba anthu amangoti nzakhunyu, koma kenako adangomva ana akulira momvetsa chisoni ndipo atathamangirako adakamupeza nsimbi yofululira kachasu ili mmanja akumenya nayo ana akewo, adatero gogo wa anawo. +Gogo Moses adati anthu achifundo adatengera anawo kuchipatala cha Lobi pomwe ena adapanikiza mayiyo ndi zibakera komanso mitengo koma atawapulumuka, adathawa nkukadziponya mumtsinje wa Luwenga womwe uli pafupi ndi mudziwo. +Gogoyu adati anthu omwe amathamangira mayiyo adamuvuula nkumutengera kunyumba koma adakathawanso nkukadziponyanso mumtsinjewo ndipo anthu odutsa adamuzindikira nkumuvuulanso ndi kukamuperekeza kwawo. +Monse zimachitika izi, akuti nkuti gogoyu ali kumunda ndipo anthu ena ndiwo adakamuuza kuti adzukulu ake awatengera kuchipatala ndipo adangouyamba kulondola. +Chichokereni moti ndilibe chithunzithunzi kuti kuli bwanji chifukwa anthu odzandiona kuno akuti chifukwa chokwiya kuti anthu adalanditsa anawo, [mayi wa anawa] adayamba kulimbana ndi nyumba yanga mpaka adagwetsa chipupa chimodzi. +Akuti sikudali bwino ndipo palibe amayandikirako. Ena adandiuza kuti adatenga musi nkuyamba kumenya nyumba yanga mpaka kugwetsa chipupa moti sindikudziwa kuti ndikatuluka ndikafikira poti? adatero gogoyo. +Adotolo pachipatala cha Lobi ataona momwe anawo adalili, akuti adaitanitsa ambulansi kudzawatenga kupita nawo kuchipatala cha Dedza kuti akalandire thandizo msanga. +Namwino, yemwe amayanganira mchipinda chogona ana pachipatalapo tsiku lomwe Msangulutso udapitako kukawaona, adati anawo adafika ali chikomokere ndipo wamngono zediyo adafikira mchipinda cha matenda akayakaya. +Sadali mwakanthu moti tidachita kumuika pa oxygen [makina ampweya] chifukwa amalephera kupuma. Mubongo mukukhala ngati mudakhuthukira magazi moti tikudikira adotolo kuti amuunikenso kuti mwina timutumize kuchipatala chachikulu cha Kamuzu Central, adatero namwinoyo. +Gogoyo adati mayi wa anawo adayamba kugwa khunyu ali ndi zaka 10 ndipo amuna okwana atatu akhala akupalana naye ubwenzi mpaka kumpatsa ana atatuwo koma amamuthawa akazindikira kuti amagwa khunyu. +Ana atatu onsewa ndamuthandiza kulera ndine ndipo ndavutika nawo kwabasi moti ndikumva kuwawa kuti iyeyo adaganiza kuchita zimenezi, adatero gogoyo. +Mkulu wake wa mayi wa anawo, Jennifer Wilson, adati anawo akachira adzawatenga chifukwa chomwe chili kumtima kwa mngono wakeyo sichikudziwika. +Ndilolera kuti ngakhale ndili ndi mavuto anga, iyeyo asadzasungenso anawa, ndidzangowatenga angadzawapange zoopsa kuposa apa chifukwa sitikudziwanso kuti ali ndi malingaliro otani, adatero Wilson. +Iye adati zitachitika izi, mayi wa anawo adamutengeranso kuchipatala chifukwa adafooka ndi mankhwala omwe adamwawo komanso chifukwa adamenyedwa kwambiri ndi anthu okwiya ndi zomwe adachitazo. +Wilson adati abale ake a mayiyo akufuna kuti achipatala akamuyeze ngati khunyulo lakhodzokera kumisala monga momwe iwo akuganizira. +Mneneri wa polisi mbomali, Edward Kabango, adati anthu adangotengera ana ndi mayiyo kuchipatala koma osakanena chilichonse kupolisi chifukwa mmabuku awo a milandu mulibe dandaulo lokhudza nkhaniyi. +Tsiku lokumbukira usodzi Chaka chino zangokumanizana ndendende kuti lero, pa 21 November, ndi tsiku loganizira nsomba ndi ntchito za usodzi padziko la pansi (World Fisheries Day). Bungwe la United Nations lidakhazikitsa tsikuli pokhudzidwa ndi kuchepa kwa nsomba komanso kusakazika kwa zachilengedwe zammadzi padziko lonse. +Patsikuli, asodzi padziko lonse amakonza zochitika zosiyanasiyana zozindikiritsa anthu kufunika kwa nsomba pamiyoyo ndi chitukuko cha maiko awo, dziko lapansi komanso kusamalira zachilengedwe zammphepete mwa nyanja. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kwathu kuno, tsikuli lidakumbukiridwa koyamba chaka chathachi pamwambo umene udachitikira mboma la Nkhata Bay. Mwambowo udakonzedwa ndi bungwe la Ripple Africa. +Miyoyo ya anthu oposa 400 000 amene amadalira usodzi paumoyo wawo ili pa chiopsezo, kaamba kochepa kwa nsomba mnyanja ndi mmitsinje ya dziko lino. Chimene chikuchitika pakalipano nchakuti pamene mitundu ya nsomba zofunika kwambiri monga chambo, kampango ndi utaka zikusowa, mpamene bonya akuchulukirachulukirabe. +Mtsogolo muno tidzafotokozera chifukwa chiyani zinthu zikubwerera chammbuyo chonchi, koma pakalipano nkofunika kulimbikitsa njira zimene zikutsatidwa poteteza nsomba kuti anthu ambiri asadzasowe pogwira zisanatheretu. +Usakhale udindo wa boma lokha komanso mafumu, asodzi eni ake, anthu wamba, mabungwe monga a Ripple Africa, USAID Pact, World Fish Centre ndi sukulu zaukachenjede kugwirana manja ndi kumaimba nyimbo imodzi poteteza nsomba. Nyanja zonse za mdziko muno zimayerekezedwa kuti zimatulutsa nsomba zoposera 50 000 tonnes pachaka, zomwe nzochepa kwambiri kukwanitsa kudyetsera mtundu wa Amalawi. Motero sizodabwitsa kuti nsomba zina zimalowa mdziko muno kuchokera kumaiko ena. +Kaamba ka kuchepa kwa nsomba, munthu mmodzi akumuyerekeza kuti akumadya makilogalamu anayi okha mmalo mwa makilogalamu 14 a nsomba pachaka. Izi zikupereka chithunzithunzi kuti ndi nsomba zochepa zimene zikumaphedwa mnyanja ndi mmitsinje ya dziko lino, motero nkofunika kulimbikitsa njira zobwezeretsanso chiwerengero cha nsomba monga kutseka kwa nyanja komanso kuyambitsa ulimi woweta nsomba mmaiwe. +Lingalirani zobzala mitengo Mvula masiku ano ikugwa mwanjomba, kutentha kukuonjeza, madzi sachedwa kuuma komanso nthaka ikukokoloka modetsa nkhawa. Awa ndi ena mwa mavuto omwe akatswiri akuti akudza chifukwa chilengedwe chikuonongedwa ndi kusasamala makamaka mmene anthu akudulira mitengo. Chaka ndi chaka mdzinja, Amalawi amalimbikitsidwa kubzala mitengo pofuna kubwezeretsa chilengedwe. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi mkulu wa bungwe la mgwirizano wa alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) Prince Kapondamgaga zokhudza ntchitoyi. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kodi a Kapondamgaga nchifukwa ninji masiku ano nyengoyi ikuoneka kuti siikupanganika? Pamenepa anthu akhoza kuzungulirapo kwambiri koma nkhani yeniyeni ndi yakuti anthu adaononga chilengedwe kwambiri ndiye momwe zinthu zimayendera kale si momwe zingamayenderenso panopa ayi. +Mukutanthauzanji pamenepa? Kapondamgaga kubzala mtengo chaka chatha Apa ndikutanthauza kuti momwe mvula inkagwera kale si momwe ingagwerenso pano chifukwa mwachitsanzo tonse tikudziwa kuti mvula imabwera chifukwa cha mitengo yomwe imasefa mpweya malingana ndi mmene zimakhalira mlengalenga. Panopa mitengo ija idatha ndiye mpweyawo usefedwa bwa? Nanga ngati mpweya si usefedwa, mvula ichokera kuti? Mukakamba za kutentha ndiye musachite kufunsa chifukwa mpweya wotentha omwe anthu ndi zinyama komanso mafakitale zimatulutsa, mitengo imayamwa nkumapangira chakudya ndipo imatulutsa mpweya womwe timapuma nkumanyadirawu koma tsopano mitengoyo kulibe nchifukwa chake kumatentha motere. +Ndiye inu mwati alimi azibzala mitengo yambiri, ndiye kuti nkhani ya mitengoyi imakhudza alimi okha? Ayi, si ntchito ya alimi okha koma munthu aliyense kungoti ambiri mwa mavuto omwe tatchulawa akukwapula kwambiri ntchito za ulimi. Chifukwa cha kutha kwa mitengo, nthaka lero ili pamtetete zomwe zikuchititsa kuti mvula ikangogwa ngakhale pangono, madzi azithamanga kwambiri nkumakokolola nthakayo moti pano chonde chambiri chidapita. +Ndiye mwati njira yake nkubzala mitengo basi? Basitu ndiye njira yake imeneyo. Komanso sikuti kubzala mitengoko ndiye kuti mukukonza kapansi muulimi okha ayi chifukwa pali ntchito zambiri za mitengo monga kutchisira fodya kwa alimi a fodya, kumangira zigafa, kuchita mapaso a nyumba, kupangira mosungira zokolola monga nkhokwe, kumangira makola a ziweto, nkhuni ndi ntchito zina zambirimbiri. +Kodi mitengoyo ikhoza kubzalidwanso mwa mthirira? Palibe vuto bola ngati munthu ali ndi madzi komanso nthawi yothirira mitengoyo koma nthawi yabwino ndi nyengo ya mvula nchifukwa chake chaka ndi chaka nyengo ya mvula kumakhala nyengo yobzala mitengo. Nyengoyi ndi yabwino chifukwa kuthirira kwake nkosavuta madzi amakhala ambiri, ntchito imakhala yongolambulira basi. Mvula ikamadzati ikutha, mitengo yambiri imakhala itagwira moti siivuta chifukwa munthu akhoza kukhala sabata zingapo osathirira koma mitengo osafa. +Kodi mitengoyo nkungobzalapo kuti bola mitengo kapena bwanji? Ayi ndithu mpofunika kuona posankha mitengo yobzala. Kusankha kumatengera ndi malo ake monga pali mitengo ina yoteteza ku mphepo ya mkuntho yomwe imafunika kukhala yamizu yozama kuti izipirira ku mphamvu ya mphepoyo. Palinso mitengo ina yoteteza nthaka yomwe imafunika kukhala ya mizu yoyanza bwino kuti madzi asamathamange kwambiri. Koma pankhani ya ulimi timalimbikitsanso kubzala mitengo yachonde yomwe alimi angakambirane ndi alangizi mmadera mwawo. +Mlimi wamba angapeze bwanji mbande za mitengo? Eya, pali njira zambiri zopezera mbande za mitengo. Njira yoyamba ndi kugwirizana pamudzi nkuona vuto lomwe lilipo ndipo mukatero mukhoza kukauza alangizi kuti akuthandizeni komwe mungapeze mbande. Njira yomweyo mukhoza kupanga pakalabu kapena munthu aliyense payekha. Kutengera upangiri wa alangiziwo, mukhoza kuona kuti muchita bwanji chifukwa pali mbande zina zomwe alimi ena amafesa nkumagulitsa zomeramera komanso mukhoza kungogula mbewu kapena kutola mnkhalango nkufesa nokha kuti pofika nyengo ya mvula mudzakhale ndi mbande. +Inuyo a bungwe la mgwirizano wa alimi mumatengapo mbali yanji pantchitoyi? Ifeyo ndi amodzi mwa magulu omwe ali patsogolo kulimbikitsa ntchitoyi moti chaka chilichonse timakhala ndi tsiku lomwe timakabzala mitengo kumalo ena ake malingana ndi pologalamu yathu. Kupatula apo, timakhalanso tikubzala mitengo patokhapatokha mmadera momwe timakhala komanso alimi ndi mabungwe ena akatiyitana kuti tikakhale nawo akakonza mwambo wobzala mitengo ife timakhala okonzeka. +Nanga monse tidayambira kubzala mitengo muja siidakwanebe? Ambuye musadzakhale ndi maganizo amenewo. Mmene anthu akudulira mitengomu mungamati yobwezeretsapo yakwana zoona? Ndiponso kunenna mosapsatira pakufunika kubzala mitengo yambiri zedi kuyerekeza ndi yomwe imabzalidwa chaka ndi chaka. Osayiwalanso kuti mitengo yomwe imabzalidwa siyonse yomwe imakula; ina imafa ndiye imafunika kubwezeretsa.n Kapondamgaga kubzala mtengo chaka chathandiwo akulima. +Katsoka: Mutu wa alakatuli Ulakatuli ndi limodzi mwa maluso omwe akuphukira kumene mdziko muno. Zaka zambiri zapitazo, anthu samatenga ndakatulo ngati njira yofalitsira uthenga kapena kuphunzitsa monga momwe zikukhalira pano. Pazaka zochepa zokha, alakatuli mdziko muno atumphuka ndipo anthu ambiri ayamba kukonda ndakatulo. Alakatuliwa adakhazikitsa bungwe lawo lomwe mtsogoleri wake ndi Felix Njonjonjo Katsoka. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere: Katsoka: Ndidayamba mu 1994 Tandiuza dzina lako ndi komwe umachokera. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ine ndine Felix Njonjonjo Katsoka. Ndimachokera mmudzi mwa Chingamba mboma la Ntcheu koma pano ndikukhala ku Nkhotakota. Ndidaphunzira za uphunzitsi koma ndimagwira ntchito ya zaumoyo kumbali ya zakudya zamagulu. +Utsogoleri wa alakatuli udaulowa liti? Ndidauyamba mchaka cha 2009. Malingana ndi malamulo athu, timayenera kukhala ndi zisankho zaka zisanu (5) zilizonse moti panopa tili kalikiriki kuthamangathamanga kuti tipeze ndalama zopangitsira nkhumano ina komwe tidzakhalenso ndi zisankho. +Kodi bungwe limeneli lidayamba liti? Bungweli lidayamba mchaka cha 1997 pomwe alakatuli adakumana kubwalo la masewero la Kamuzu Stadium. Ena mwa akatakwe omwe adali kumeneko ndi monga Laurent Namarakha, malemu Aubrey Nazombe, Edward Chitseko ndi malemu George Chiingeni. Pa 4 September, 1998, bungweli lidalembetsedwa kunthambi ya kalembera wa mabungwe. +Cholinga chake nchiya? Cholinga cha bungweli ndi kufuna kutukula luso la ulakatuli mMalawi muno komanso kufuna kufalitsa mauthenga ndi kuphunzitsa anthu kudzera mndakatulo monga momwe amachitira azisudzo kapena oyimba. +Iweyo udayamba liti ndakatulo? Ndidayamba ulakatuli mchaka cha 1994 ndili pasukulu ya sekondale ya Likuni Boys. +Uli ndi masomphenya anji pa ndakatulo mmalawi muno? Masomphenya anga ndi akuti ndakatulo zidzafike pabizinesi ngati momwe maluso ena alili pano. Kuti izi zidzatheke mpofunika kupeza akatswiri oti adzatithandize moti boma ndi mabungwe atalowererapo zikhoza kutithandiza kwambiri. Njira ina ndi yakuti alakatuli onse azilembetsa ntchito zawo kubungwe la Cosoma kuti tizitha kukhala ndi chithunzithunzi chenicheni cha chiwerengero cha alakatuli omwe tili nawo. +Anatchezera Akumandiipitsa Zikomo agogo, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndili ndi chibwenzi ndipo makolo akudziwa ngakhale kuti ndi mwamphekesera chabe. Nthawi ina bambo ake (osati omubereka) amafuna kumugwiririra ndiye akumandiipitsa dzina kwa mayi ake, koma iwo sakutekeseka ndi izi. Ndili ndi mantha, nditani pamenepa agogo? FK, Mchinji FK, Wati uli ndi mantha, mantha ake otani? Sindikuonapo chifukwa choti uzikhala ndi mantha pamene sudalakwire munthu aliyense. Ndiye iwe ukuchita mantha ndi ndani? Ngatidi ukunena zoona kuti bambo omupeza a mtsikanayo adafunadi kumugwiririra, bwenzi lakolo adachitapo chiyani zitachitika zimenezo? Kodi mayi a mtsikanayo nkhaniyi akuidziwa? Ngati akuidziwa adachitapo chiyani? Ndikufunsa mafunso onsewa chifukwa ndi mlandu waukulu kugwiririra kapena kufuna kugwiririra ndipo munthu wopalamula mlandu wotere amayenera kulangidwa kundende malinga ndi malamulo a dziko lino. Munthu wotere ngosafuna kumusekerera. Ndibwerere kunkhani yako yoti uli ndi mantha. Ngati umamukonda zoona mtsikanayo pitiriza kutero chifukwa tsiku lina udzakhala mpulumutsi wake kwa bambo womupezayo mukadzakhala thupi limodzi. Mwina mayi ake sakutekeseka ndi zokuipitsira dzina lako chifukwa akudziwa choona chenicheni, maka pankhani yoti amuna awo amafuna kugwiririra mwana wawo, koma akukhala chete chifukwa akuopa kuti angawasiye banja. Tazionapo izi zikuchitika. +Akuti tibwererane Zikomo gogo, Ndinali pachibwenzi ndi mtsikana wina kwa miyezi isanu ndi umodzi. Pamene timati tipange ukwati mwezi wotsatira iyeyo adathetsa chibwenzi ndi kutengana ndi wina. Patatha miyezi iwiri adabwera ndi kudzandipepesa ati tibwererane koma akwathu akukana. Kodi nditani pamenepa? NG, Mzuzu NG, Utani pamenepa? Mvera malangizo a makolo ako kapena akwanu amene akuti usayerekeze kubwererana naye chifukwa zimene akukulangizazo ndi zoona. Mawu a akulu amakoma akagonera, ukanyalanyaza udzalirira kuutsi tsiku lina. Iye adathetsa chibwenzi pakati pa iwe ndi iye ndipo adakwatiwa ndi wina kenaka patha miyezi iwiri uyo akubwera poyera ali undikhululukire, tibwererane. Alibe manyazi! Chavuta komwe adakakwatiwako ndi chiyani? Chilipochilipo. Ndiye iwe ukavomereza zoti mubwererane udzaoneka wombwambwana; wodya masanzi. +Ndimukhulupirire? Agogo, Ndili pachibwenzi ndi mnyamata wina wake. Ndakhala naye zaka zinayi. Chaka chino adakaonekera kwathu koma ineyo akundikaniza kuti ndikaonekere kwawo. Ndikamufunsa kuti akundikaniza chifukwa chiyani sayankha zogwira mtima koma ndikamufunsa za ukwati amavomera ndi mtima wake wonse. Ndimukhulupirire? Ine Fannie, Blantyre. +Bwanji nkhuku yoweta sagula pamsika? Achewa ali ndi njira zosiyanasiyana zoperekera malango pakati pawo. Njira zina ndi monga nthano, magule, ndakatulo, chinamwali ndi miyambi ndi zininga. Lero nkhani yathu yagona pa miyambi ndipo tifukula mwambi wakuti nkhuku yoweta sagula pamsika. STEVEN PEMABMOYO adacheza ndi mfumu yaikulu Njewa ya ku Lilongwe, yomwe ikutambasula za mwambiwu. +Choyamba, mfumu, tafotokozani za momwe nkhani ya chikhalidwe cha makolo ilili kuno. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kwathu kuno ndi dera limodzi lomwe anthu sataya chikhalidwe cha makolo ndipo kuti mukhale pakati pathu kwa masiku angapo mukhoza kuona kusintha poyerekeza ndi zomwe mudazolowera kuona. Anthu a kuno adamva mwambo ndipo adausunga. +Njewa kufotokoza za tanthauzo la mwambiwo Tsono mukati adamva mwambo mukufuna kunena kuti adaumva bwanji? Pakati pa Achewa, mwambo ndi chuma chosiyirana. Makolo kalero adasiyira ana awo omwe adasiyiranso ana awo chonchoo mpakana lero timangosiyirana kuti mpakana kalekale mtundu wathu usadzasokonekere ayi. +Ndikufuna kudziwa kusiyiranako mumachita kupatsana pamanja? Ayi, mwambo si chithu choti mungachione kapena kuchigwira. Imakwana nthawi yoti makolo amadziwa kuti mwana uyu akufunika kudziwa zakuti ndiye amakonza njira yomupatsira mwambo womwe ukufunikawo. Pali njira zingapo monga kutengera mwana kutsimba, kudambwe, kumuitanira anamkungwi kapena kudzera mmiyambi yomwe amatolamo tanthauzo. +Eya pamenepo, pali mwambi uja amati nkhuku yoweta sagula pamsika. Mwambi umenewu uli ndi tanthauzo ndithu? Kwabasi, mwambi umene uja uli ndi tanthauzo lozama kwambiri ndipo mwachita bwino kusankha mwambi umenewu chifukwa umakhudzana ndi moyo wa munthu, makamaka akakula, kuti akukalowa mbanja nkukayamba moyo wina. +Ndikufuna mumasule bwinobwino kuti nkhuku ikubweramo bwanji. +Chabwino, ndiyambe ndi kumasulira motere: munthu ukafuna nkhuku yoti uwete, supita pamsika chifukwa akhoza kukugulitsa yodzimwera mazira kapena yoti idatopa kale kuikira ndiye kuti palibe chomwe wachitapo. Pokagula nkhuku yoweta umafika pakhomo pomwe pali khola ndipo umafunsa umboni woti nkhukuyo ikadaikira kapena isadayambe nkomwe ndipo kuti mtundu wake umaikira motani. Apa zimatanthauza kuti munthu akafuna banja sangangopita pamsewu nkutengana ndi mkazi kapena mwamuna osadziwa mbiri yake, komwe amachokera ndi mtima wake. +Koma amayenera kutani? Munthu wanzeru amayenera kupita kwa makolo kapena abale a munthu yemwe wamukonda kukaonako ndi kuphunzira khalidwe lawo. Akhozanso kufufuza kudzera kwa anthu adera omwe amakhala kufupi ndi munthuyo, akakhutira akhoza kuyambapo dongosolo. Izi ndi zomwe makolo amatanthauza mmwambiwu. +Paliso pena pomwe mwambiwu ungagwire ntchito? Kwinako zikhoza kutengera kuti pali nkhani yanji koma bola tanthauzo lake likhale loti pakufunika kusamala, makamaka kuchita kafukufuku osangophwanyirira pochita zinthu. Koma gwero lenileni makolowo poyambitsa mwambiwu adayambitsira nkhani ya maukwati. +Akumanga mvula ndani? Tsikulo pa Wenela padali kutentha osati masewera. Zimachita kukhala ngati dziko likutha, Jahena akutsikira pansi pompano. +Nchifukwa khamu lidafika apo lidali kukonkha kummero. Mkulu wina adafika ndi mwana wake amenenso amamwa chakumwa chake. Mwanayo adali kutuluka thukuta ngati mtsinje wa Shire, inde uja wauma kuti magetsi avute chonchi. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Nanga magetsi kuzima 5 koloko mmawa, nkuyaka 12 koloko usiku, amenewa akuganiza kuti mfiti nazo zimalira magetsi? Tikudabwa zedi kuti nchifukwa chiyani kampani imeneyi kukadali ogwira ntchito. Amachitako chiyani? Mwana adazunzika nalo thukuta, limene limatsikira mmasaya. +Adapukuta thukuta, koma ngati alire. +Amvekere: Daddy, I am melting! Ana amasiku ano Chingerezi! Ndikumbuka masiku amenewo ndisanatulukire pawindo kusukulu kwathu kwa Kanduku, Chingerezi chimene ndinkadziwa ndi please teacher mayi go out basi! Ndiye ndikumva kuti Moya Pete anadzibera yekha zikwama paja anagona padepoti! adayamba milandu ina Abiti Patuma. +Kaya nkhanizi amazitenga kuti? Tonse tidangoti kukamwa yasaaa! Moya Pete simukumudziwa, nthuni. Wadzibera yekha zikwama kuti muone ngati akuvutika, adapitiriza. +Aliyense maganizo adali pakutentha. Adatulukira Moya Pete wa Dizilo Petulo Palibe, Lazalo Chatsika wa Male Chauvinist Pigs komanso Atipatsa Likhweru wa Ukafuna Dilu Fatsa. Amene padalibe ndi Adona Hilida aja adathawa nkhondo ya Angitawo. +Onsewo thukuta lili kamukamu. +Koma kutentha kumeneku bwanji? Akumanga mvula ndani kwambiri? adafunsa Moya Pete atakhalira kereti. +Nzochita kufunsa? Mukumanga mvula ndinu. Tangomva kuti mwaotcha uvuni kuti nanunso mumange nyumba ya manda momwemo muja adachitira Mfumu Mose, adatero Lazalo. +Moya Pete adakwiya kwambiri. +Koma udzasiya makani, iwe? Tonse tikudziwa kuti ukumanga mvula ndiwe. Cholinga chako pano pa Wenela anthu asalime, adzavutike ndi njala kenako udzandichotse pampando. Wagwa nayo kwambiri, adatero iye. +Atipatsa adangoseka: Zoona iwe, Lazalo, wamanga mvula. Ukufuna ukalawe kumpanda. Ulira. Uli ndi mwayi gogo wanga Che Polamani adapita. +Zikugwirizana bwanji? adafunsa Abiti Patuma. +Enanutu mwina simukuwadziwa Che Polamani. Adali singanga wovuta zedi. Amatha kuyala mphasa pamstinje nkumaothera dzuwa koma osamira. Inde, ankatha kuyanika malaya mmalere popanda dzuwa. +Posakhalitsa idatulukira nyakwawa Wenela. Nyakwawayo imasowa kwambiri, tidadabwa kuti idatilemekeza bwanji tsikulo. +Ndamva mukukangana za mvula. Musadandaule, tikuimanga ndife. Zaka zonsezi mumatipatsa ife nzika zitupa zogulira feteleza, chaka chino mwatimana ndiye tiona kuti mvula yanuyo ichokera kuti, idatero mfumuyo. +Tonse tidangoti kukamwa kakasi. +Kapena tipite ku Khuluvi tikathire nsembe kwa Mbona? ndidafunsa. +Onse adangoseka, kudzimvera chisoni. +Bzalani mbewu zocha msangaLipita Woyendetsa ntchito za ulangizi ndi njira zamakono za ulimi muunduna wa zamalimidwe, Wilfred Lipita, wati alimi akuyenera kutengerapo phunziro pa zomwe zidaoneka muulimi wa chaka chatha ndi kusankha mwanzeru mbewu zolima chaka chino. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Polankhula ndi Uchikumbe paulangizi, Lipita adati masiku ano nkovuta kutchera kuti mvula iyamba lero ndipo idzatha mawa mmalo mwake njira yabwino nkusankha mbewu zocha msanga. +Upangiri wa zanyengo ndi umenewo komanso payekha mlimi ayenera kukhala wozindikira kumwamba kukhoza kusintha nthawi iliyonse malingana nkusintha kwa nyengoku, adatero Lipita. +Lipita: Alimi ena apulumukira chinangwa Iye adati kunjaku kuli mbewu zocha msanga zomwe mvula itati yadulira panjira, mlimi akhoza kupeza popumira kusiyana nkukakamira mbewu zokhalitsa mmunda chifukwa izi ndizo zingalowetse njala. +Mkuluyu adatinso pomwe alimi akubzala mbewu zachizolowezi monga chimanga, nyemba, fodya ndi zina ayeneranso kulingalira za mbewu zina zopirira kuchilala monga chinangwa ndi mbatata. +Mu ulangizi wake, Lipita adati alimi ena chaka chino apulumukira chinangwa ndi mbatata kupatula ulimi wa mthirira malingana nkuti ulimi chaka chatha sudayende bwino chifukwa cha mvula yokokolola ndi ngamba. +Mbewu ngati chinangwa zili mgulu la mbewu zomwe timati zachitetezo chifukwa ngakhale mvula idule, izo zimaberekabe. Palibe kanthu kuti mitsitsi yake ndi yaikulu kapena yochepa bwanji koma nkhani ndi yakuti mbewu zina zitakanika, mlimi amakhala ndi pogwira, adatero Lipita. +Mmadera ambiri chimanga chidatuluka ndipo mlangizi wamkuluyu adati imeneyi si nkhani yokhazikika pansi koma kulimbikira ntchito za mmunda monga kupalira kuti mbewu zisamalimbirane chakudya ndi udzu. +Iye adati mbewu zokulira mtchire zimanyozoloka ndipo sizibereka bwino ngakhale mlimi ataononga ndalama zambiri kugulira feteleza. +Omwe chimanga chawo chatuluka, ino ndiye nthawi yoyamba kulingalira kupalira ndipo chikafika mmawondo ndi nthawi yothira feteleza wina ndi kubandira kuti chinyamuke ndi mphamvu, adatero Lipita. +Iye adati chimanga chikanyamuka ndi mphamvu maberekedwe ake amakhala osiririka ndipo mbewu yake ikakhala yabwinonso, phesi limodzi limabereka chiwiri kapena chitatu podzakolola nkudzakhala ngati minda iwiri pomwe udali umodzi. +Kasambara: Akhazikitsa chimbale mwezi uno Martha Kasambala ndi woimba nyimbo zauzimu ndipo amakhala ku Mzuzu. Iye ali ndi zimbale ziwiri ndipo mu December muno akuti akhazikitsa chimbale chake chatsopano chotchedwa Amasamala. Mtolankhani wathu DAILES BANDA adacheza naye motere: Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ali ndi uthenga wapadera mchimbale chatsopano: Kasambara Tikudziweni Ndine Martha Kasambara wa mmudzi mwa Malanda ku Chintheche mboma la Nkhata Bay. Ndili pabanja ndipo ndili ndi mwana mmodzi. +Mbiri yako pamaphunziro njotani? Ndidaphunzira pulaimale yanga pa Lilongwe LEA pomwe ndidalemba mayeso anga a Standade 8; sekondale ndidaphunzira ku Chipasula ku Lilongwe komweko. Ndidakapanga maphunziro a zauphunzitsi ku Tanzania komwe ndidaphunzitsa mwakanthawi pangono ndipo pakadalipano ndikupanga bizinesi. +Ndiye zoimbaimbazi mudayamba bwanji? Ndidayamba kuimba ndili wachichepere kwambiri koma chimbale changa choyamba ndidatulutsa muchaka cha 2008 chomwe chimatchedwa kuti Zonse ndi Yesu. Chimbale chachiwiri Nganganga ndi Yesu chidatuluka mu 2010. Chimbale chatsopano chotchedwa Amasamala ndichikhazikitsa mu December muno. +Uthenga waukulu womwe wanyamula ndi wotani mchimbalechi? Kwakukulu uthenga omwe uli mchimbalechi ndi wachilimbikitso kwa Akhristu anzanga munyengo zili zonse zomwe iwo akudutsamo. Yesu amasamala anthu ake ndipo tikamudalira iye sitidzakhumudwa chifukwa chisomo chake ndi chokwanira. +Kodi mfundo za munyimbo zimenezi mumazitenga kuti? Nyimbo zanga kwambiri zimachokera pa maulaliki a kutchalitchi komanso ndikamawerenga Baibulo ngakhalenso nthawi zina zinthu zomwe ndikuona ndi kukumana nazo. +Ndi zinthu ziti zomwe mungakonde kuti zisinthe kumbali ya zoimba mMalawi muno? Mmastudio mwathu mukufunika zipangizo zamphamvu zojambulira nyimbo ngati mmene kulili kumaiko a anzathu, monga ku South Africa, chifukwa nyimbo zimamveka bwino kwambiri. +Phindu mukulipezamo mukuimbaku koma? Mmbuyomu zinthu zimavuta koma pakalipano ndi chimbale chatsopanochi, tsogolo lopindula likuoneka. +Zaka zinayi kwa ofuna kuba alubino Njonda ziwiri zochokera mboma la Mzimba Lachitatu zidagamulidwa kukasewenza jere kwa zaka zinayi ndi kugwira ntchito yakalavula gaga chifukwa chofuna kuba ndi cholinga chopha mwana wa chialubino wa zaka zinayi wa mwamuna. +Lusungu Sele wa zaka 30 ndipo amachokera mmudzi mwa Mkoko, T/A Chindi ndi Jailosi Luwanda wa zaka 24, wochokera mmudzi mwa Vakalani kwa Senior Chief Mtwalo adanyengerera bambo womupeza wa mwanayo kuti amube pamtengo wa K20 miliyoni. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Koma bwalo la milandu la Mzuzu pa 21 Decemberlidamasula bamboyo, Christopher Kumwenda wa zaka 38 yemwe amachokera mmudzi mwa Kumwenda, T/A Mzikubola mboma la Mzimba, ati popeza padalibe umboni wokwanira woti adali ndi cholinga chogulitsa mwana wake womupezayu. +Apa nkhaniyi idatsalira Sele ndi Luwanda. +Ndipo wapolisi woimira boma pamilandu Lloyd Magweje adauza bwalolo kuti Sele adalumikizana ndi Luwanda yemwe amakhala ku Mzuzu kuti ndiye adzagule mwanayo diluyo ikatheka. +Bwaloli lidamva kuti mphepo za chiwembuchi zitamupeza mayiyo adathawitsa mwana wakeyu kupita naye mmudzi mwa Chisewe, mboma lomwelo. +Koma pa 25 August chaka chatha, Sele adatsatira mwanayu mmudzimu pomwe adali kusewera pagulu la anzake. +Apa diluyo idapheduka popeza Sele adayamba wafunsa wachibale wa mwanayo za momwe angamupezere; ndipo wachibaleyu adakatsina khutu mayi wa mwanayo yemwe adakanena kupolisi kuti akusakidwa. +Ndipo Magweje adapempha bwaloli kuti liwapatse awiriwa chilango chokhwima chifukwa milandu yotere ikuchulukira komanso mwanayo adasiya kusewera ndi anzake ndipo amatsekeredwa mnyumba. +Podandaula, Sele adauza bwalolo kuti limupatse chilango chozizira poti amasamala banja lake pamene Luwanda adati ndi wamasiye komanso amasamala mkazi ndi ana ake awiri. +Poweruza, majisitileti Tedious Masoamphambe adati chilango chomwe abwalo amayenera kupereka chimafunika chikhale choti anthu akhutitsidwe nacho kuti chithandiza kuteteza ma alubino omwe akuphedwa ndi kuchitidwa nkhanza. +Masoamphambe adati komabe chilangochi chimafunika chikhale chogwirizana ndi mlandu kuti anthu asaganize kuti awiriwa alangidwa mwankhanza. +Ndili ndi chikhulupiliro kuti chilangochi chiwasintha kukhala nzika zabwino, Masoamphambe adatero asadapereke chigamulocho. +Koma chigamulochi sichidasangalatse bungwe loona za ufulu wa alubino la Association of People with Albinism in Malawi. +Mtsogoleri wa bungweli Bonface Massa adati akadakonda akadapatsidwa zaka zosachepera 14. +Kuchitsedwa ntchito ndi zina Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mourinhao ndi mmodzi mwa anzanga amene ndimacheza nawo pa Wenela. Sindikudziwa kuti nchifukwa chiyani mkuluyu amakonda Arsenal. Momwe amaonekera, nzeru zake, ndimadabwa kuti iyeyu ndi Arsene Wenger adadyetsana mankhwala a mtundu wanji. +Nchifukwa chake nthawi zambiri tikamukumbutsa kuti patha zaka 10 timu yakeyo isanachite zakupsa potenga chikho amakwiya zedi! Koma iyo ndi nkhani ya tsiku lina. +Tsono Mourinhao adatopa ndi kuitanira minibasi, ndipo adapempha mwini minibasi ina kuti amupezere ntchito. Mwini minibasiyo adali dotolo. Pambali pothandiza odwala ku Gulupu, dotoloyo amakaphunzitsanso kusukulu ina ya anamwino. +Apa zili bwino Tade. Kukhosi kwanga kuchita kusalala. Bakhalani ndi kuitanira kwanuko mpaka day yobwera Yesu. Uku kukumakhala kudya za tswayitswayi osati masewera, adandiuza tsiku lina atatizungulira pa Wenela. +Koma ngati adathako sabata zitatu? Ndidangoona akubwera tsiku lina atazyolika. +Bwanjinso nanga? ndidamufunsa. +Ndailephera ntchito. Andichotsa, adayankha mwa chidula. +Apa mpomwe adafotokoza momwe ntchitoyo idathera. +Ndimagwiranso ntchito yokonza mnyumba mwa dotoloyo: kukolopa, kusesa, kukonza mufiliji ndi zina zotero. Tsiku lina, ndidapeza kuti liver ina idakhalitsa mfilijimo. Ndidaaitenga kukaotcha kunyumba. Atabwera mkulu uja adandifunsa: Ndinasiya katundu umu, watenga ndani? Ndipo ndidati sindikudziwa, adafotokoza mkulu uja. +Adamezera malovu, nkupitiriza: Nthawi ya nkhomaliro adandifun-sanso, ndidakananso. Ngakhalenso madzulo adandifunsa ngati ndidaona katundu wake, ndidakananso. Pobwera madzulo tsiku linalo, adabwera ndi mowa umene adandigaila. +Akuti mkuluyo ataona kuti Mourinhao wayamba kuledzera adamufunsanso: Ndinasiya katundu wanga. Watenga ndani? Ndipo Mourinhao adayankha: Mukunena nyama ija? Ndaotchera, pepani. +Mkulu uja adangoti: Chinalitu chiwindi cha munthu ndimati ndikaphu-nzitsire. +Abale anzanga, tikakhala pantchito sib wino kusolola ngakhale zimene tikuziona kuti nzazingono. Tikadakhala kuti tonse tilibe mtima osolola, nkhani ngati zotengera abale ndi alongo kunja moononga ndalama, kubwereka ndege yaufiti ngati kabanza si bwenzi zikutisautsa. +Hallo Tade, wasowatu. Ndalanga wina uku, adatero Abiti Patuma, msungwana wosowa ngati Adona Hilida pano pa Wenela. +Zinakhalanso bwanji? adafunsa Gervazzio, mmalo moika nyimbo ya Nakulenga. +Amakula mtima, ati mkazi wake amamukhulupirira koopsa ndipo iyeyo kanali koyamba kuti apusitse mkazi wakeyo pocheza ndi ine. Poti anali ataledzera modziiwala, ndinatenga mapepala onse amagwiritsa ntchito nkuwaika mthumba la buluku, adatero Abiti Patuma. +Adaonjeza kuti mawa lake, adangomva kuti ukwati wamkuluyo watha. +Za ukamberembere mu Fisp akuti zichepe chaka chino Ntchito yotumiza zipangizo zaulimi zotsika mtengo mupologalamu ya Farm Input Subsidy Programme (Fisp) ili mkati koma nyengo ngati iyi atambwali ofuna kulemera mnjira zachinyengo amachuluka. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Atambwali oterewa akuti amalowerera msika wa zipangizozi ndi njira zosiyanasiyana ndipo pamapeto pake zipangizozi zimakathera mmanja mwa anthu ochita bwino kale mmalo mwa anthu ovutika omwe ndi eni pologalamuyi. +Apolisi, unduna wa malimidwe ndi bungwe la mgwirizano wa alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) ati chaka chino salekerera zachinye za mtundu uliwonse mupologalamuyi kuti anthu oyenerera okha ndiwo apindule. +Alimi ena mchigawo cha kumwera monga awa ayamba kale kugula zipangizo zotsika mtengo Kumbali yathu, tilimbikitsa chitetezo potumiza apolisi ambiri mmadera ndi mmisika yomwe pologalamuyi ikuchitikira. Tigwira ntchitoyi kudzera mu nthambi yathu ya chitetezo cha mmudzi ndipo ndikunena pano takonzeka kale, adatero wachiwiri kwa wamkulu wa polisi mdziko muno Rodney Jose. +Iye adati mmene pologalamuyi imayamba, boma lidapereka mphamvu zoyanganira chitetezo cha zipangizo zotsika mtengozi mmanja mwa apolisi ndipo amaigwira mogwirizana ndi unduna wa zamalimidwe ndi bungwe la alimi la FUM. +Chiyambireni pologalamu iyi, tagwirapo akamberembere ambiri. Milandu yambiri imakhala yokhudzana ndi anthu kupezeka ndi makuponi achinyengo, ziphuphu ndi kuzembetsa zipangizozi ndi cholinga chokagulitsa kumaiko akunja, adatero Jose. +Mlembi wamkulu muunduna wa zamalimidwe Erica Maganga adati ndi udindo wa mafumu ndi anthu awo kutsina khutu akuluakulu akaona mchitidwe wokayikitsa pakagawidwe, kagulitsidwe ndi kapezedwe ka zipangizozi. +Maganga adati boma limaononga ndalama zambiri mupologalamu ya sabuside ncholinga chotukula alimi ovutika ndipo ngati zipangizozi sizikuwafikira ndiye kuti zolinga za boma sizikukwaniritsidwa. +Anthu ndiwo amaona zomwe zimachitika mmadera mwawo ndiye iwo ndi amene angakhale oyambirira kukanena kuti akamberemberewo agwidwe ndipo zipangizo zawo zaulimi zipulumuke, adatero Maganga. +Ophunzira asanu anjatidwa ku Nkhotakota Apolisi Lolemba adamanga ophunzira asanu a sukulu ziwiri za mboma la Nkhotakota ndi kuwatsegulira mlandu wofuna kudzetsa chisokonezo. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mneneri wa polisi mbomalo, Williams Kaponda, adatsimikiza za kutsekera mchitolokosi kwa ophunzira anayi a pasukulu yoyendetsedwa ndi mpingo wa Anglican ya Bishop Mtekateka Private ndi wina wa sukulu ya sekondale yoyendera ya Linga Community Day Secondary School. +Kaponda adati mwa anayi amene adanjatidwa kusukulu ya Bishop Mtekateka, mmodzi ndi mtsogoleri wa anyamata pasukuluyi (headboy) Morton Mzumara, wa zaka 19. +Utsogoleri wa sukuluyi udachotsa headboy pamene iye amalankhula kwa ophunzira anzake za aphunzitsi amene adamuphwanyira iPad, adatero Kaponda. Malamulo a sukuluyi amakaniza mwana aliyense kubwera ndi foni ndipo ichi nchifukwa chake mphunzitsiyo adali ndi mphamvu zomuphwanyira foniyo. +Iye adati kuchotsedwa kwa Mzumara kudabala ziwawa chifukwa mogwirizana, ophunzirawo adafuna akuluakulu a sukuluyi afotokozepo bwino. +Pamene timalemba nkhaniyi nkuti sukuluyi itatsekedwa ndipo malinga ndi Kaponda, ikuyembekezereka kutsekulidwa Lolemba lino pamene ophunzira aliyense wapemphedwa kukabwera ndi makolo ake. +Mkulu wa mgwirizano wa makolo ndi aphunzitsi wa Parents Teachers Association (PTA) Luka Matchiya, wati kafukufuku ali mkati kuti apeze zomwe zidaonongeka pamene ophunzirawo adayamba kuswa zinthu chifukwa cha kuchotsedwa kwa anzawowo. +Ophunzira amene anjatidwawa ndi Mzumara wa mmudzi mwa Chinguluwe kwa T/A Kalonga mboma la Salima, Brave Mbewe, 20, wa mmudzi mwa Kamange kwa T/A Malengachanzi ndi Mwayi Kalozi, 19, wa mmudzi mwa Matiki kwa Senior Chief Kanyenda mboma la Nkhotakota. +Kusintha kwa nyengo kwasokoneza ulimi wa khofi Pamene mlimi aliyense akudandaula ndi kusintha kwa nyengo, nawo alimi a khofi sadasiidwe pamene zadziwika kuti dziko lino likukolola khofi wochepa chifukwa cha kusokonekera kwa nyengo. +Malinga ndi tsamba la pa intaneti la www. mzuzucoffee.org, dziko lino limayembekezereka kumakolola matani 20 000 a khofi koma chifukwa cha kusintha kwa nyengo, dziko lino likungokolola matani 1 500 okha pa chaka. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kusintha kwa nyengo kwachititsa ulimi wa khofi kulowa pansi Polankhula ndi Uchikumbe, mkulu wa kampani ya Mzuzu Khofi, Harrison Kalua, chaka chino chokha dziko lino likolola matani 1 200 okha a khofi kusiyananso ndi 1 500 amene timayenera kukolola pachaka. +Malinga ndi iye, izi zikusokonezanso kuti ulimiwu usabweretse ndalama zochuluka malinganso ndi kusokonekera kwa ndalama ya dziko lino ya kwacha. +Alimi a khofi akulira mosalekeza chifukwa chosakhazikika kwa ndalama ya dziko lino, adatero iye. +Iye adatinso alimi mdziko muno ali ndi kuthekera kolima khofi wambiri koma vuto ndi kusintha kwa nyengo komwe kukusokoneza ulimiwu zomwenso zachititsa kuti dziko lino lizikolola khofi wochepa. +Malekodi a mwezi wa September amene apanga a Coffee Association of Malawi, akuonetsa kuti dziko lino latumiza kunja makilogalamu 375 800 a khofi mmwezi wokhawu. +Malekodiwa akuti giledi yachiwiri ya khofi wa Floaters ndi Mbuni sadatumizidwe kunja kuti akagulitsidwe. +Alimi amayenera avomereze mitengo yomwe apatsidwa kuti awagulire ngati akhutitsidwa nayo. +Khofi wambiri akulimidwa mma esiteti a mmaboma a Thyolo, Mulanje, Zomba, Mangochi. Padakalipano alimi pafupifupi 4 000 ndiwo akulima mbewuyi mdziko muno ndipo alimiwa ali mmakopaletivi 6. +Njovu ipha mlenje Tsoka sasimba. Akanadziwa mlenje sakadapita kunkhalango ya Liwonde kukasaka nyama mozemba masiku apitawo. +Patrick Maya, wa zaka 52, ndipo amachokera mmudzi mwa Chipala, Senior Chief Kawinga mboma la Machinga, koma adasamukira mmudzi mwa Wadi, Senior Chief Liwonde komwe amakhala ndi banja lake adafa njovu itamuponda. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Malinga ndi mchimwene wa Maya, Maxwell Makina, iye adali ndi chizolowezi chosaka nyama mozemba pogwiritsanso ntchito agalu ake mnkhalango ya Liwonde. +Makina adati pa tsiku la tsokali, Maya adalowa mkhalangoyi komwe sadabwererenso. +Iye adati ngakhale nkhani ya kusowa kwake idawapeza abalewa mmudzi mwa Chipala laMulungu lapitali, akukhulupilira kuti mlenjeyu adaphedwa pa Khirisimisi. +Thupi lake lidapezeka Lamulungu pa 27 December, litaonongeka kale moti tidangosunga patchire pomwepo, Makina adatero. +Wachiwiri kwa mneneri wapolisi kuchigawo cha ku mmawa Otilia Kumanga watsimikiza za imfayi. +ANATCHEZERA Nditenge uti? Anatchereza, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Munthune ndili ndi zibwenzi ziwiri. Zonsezi zidayamba chaka chimodzi panopa zatha zaka zitatu ndipo onsewa ndimawakonda chimodzimodzi inenso onsewa amandikondanso. Ndiye panopa ndapanga chiganizo chokhala ndi mmodzi. Ndipanga bwanji pamenapa? Ine Zochenana A Zochenana, Akamati ichi chakoma ichi chakoma pusi anagwa chagada kapena kuti mapanga awiri avumbwitsa mumati akutanthauzanji? Ndi zimenezitu. Mwagwiratu njakata pamenepa chifukwa chosakhutitsidwa ndi bwenzi limodzi. Mwina mumayendera ija amati have many but choose one. Mphotho yosakhulupirika ndi imeneyo, achimwene. Ndanena kuti ndinu wosakhulupirika chifukwa kwa zaka zitatu mwakhala mukuyendetsa zibwenzi zanu pozinamiza kuti ndiwe wekha pamene mulinso ndi wina amene mukumuuzanso kuti ndiwe wekha. Nanga tinganene kuti zibwenzizo zikudziwana ngati? Ndakaika kuti zikudziwana. Koma ndikuthokozeni kuti tsopano mwapanga chilinganizo choti mukhale ndi chibwenzi chimodzi. Izi ndiye zotamandika chifukwa mwaonetsa kukula. Kaya mukufuna kukwatira tsopano-ngati simunakwatire kale? Ndiye zikafika apa pamakhala matatalazi kusankha chifukwa mukuti onse mumawakonda chimodzimodzi. Koma mukunena zoona? Zingatheke zimenezo kukonda anthu awiri chimodzimodzi? Zimalephera olo ana ako obala wekha umatha kusiyanitsa chikondi ngakhale mwina suonetsera. Ndiye apa tangolimbani mtima, musankhe amene ali ndi makhalidwe oyenera kulowa naye mbanja. Penapake ayenera kusiyana ndithu. Palibe amene angakusankhireni, koma inu nokha, a Zochenana. Ndili ndi chikhulupiriro kuti simunapulupudze zoti mwina muli ndi ana ndi zibwenzizo. Apo ndiye zingakuvuteni kusankha koma ngati mudadzigwira sipangakhale vuto lenileni kusiyapo mmodzi. Zimachitika koma si mmene zimayenera kukhalira, abale. +Ndili pasukulu Agogo, Ndine mtsikana wa zaka 17 ndipo ndili pasukulu. Ndili ndi chibwenzi koma mnzangayo akuonetsa kuti sakukondwera nane ndiye ndimafuna kuti mundithandize maganizo kuti ndiziwerengerabe kapena ayi? Chonde ndithandizeni. +Iwe mtsikana, Ukufuna ndikuthandize motani poti wanena kale kuti mnzakoyo akunetsa kuti sakukondwera nawe? Chomwe ndingakulangize nchoti zisiye za chibwenzizo ndipo ulimbikire sukulu. Sukulutu ndi yofunika kwambiri ndipo uike patsogolo, zina zonse pambuyo. Udakali mwana wamngono tsono zoyamba zibwenzi nzachiyani? Sukulu ndi zibwenzi siziyenderana. Ngati ufuna kuti sukulu ikuyendere usamataye nthawi nkuganiza za zibwenzi chifukwa mmalo moti uzimva zimene aphunzitsi akuphunzitsa uzingoganiza za bwenzi lakolo, osamva olo chimodzi, mapeto ake 0 pa 10! Atsikana ambiri sukulu imawakanika chifukwa cha nzeru ngati zakozo-kuika mtima pa zibwenzi. Kaya, zakozo! Usankhepo chimodzi ngati ufuna zako zikuyendere. Mwina bwenzi lakolo sakukondwera nawe chifukwa uli pasukulu ndiye akufuna usiye sukulu kuti uike mtima wako wonse pa iye. Koma ine ndikadakhala iweyo ndikadasankha sukulu, chibwenzi pambuyo. +Sakundipatsa ulemu Ndine mwamuna wapabanja mkazi ndi wachiwiri koma sandipatsa ulemu chifukwa makolo ake ndi ochita bwino. Ndili naye mwana mmodzi. Kodi nditani kuti azindipatsa ulemu monga kale? Achimwene, Ulemu sachita kupempha! Umanena chatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke mnyanga. Lero ndi lero basi mkazi wanu wayamba mwano, osakupatsani ulemu poti makolo ake ndi ochita bwino? Chilipochilipo chimene chimamupangitsa mkazi wanu kuti asakupatseni ulemu, osati chifukwa makolo ake ndi olemera. Mwina adayamba akuuzani kuti sangakupatseni ulemu chifukwa makolo ake ndi olemera? Ayi ndithu, munene chifukwa china, osati chimenecho. Mwanena nokha kuti poyamba ankakupatsani ulemu wonse, koma pano wasiya kutero, mukutanthauza kuti poyambapo makolo ake sadali ochita bwino? Koma simukunena bwinobwino ulemu umene mumafuna kuti mkazi wanu azikupatsani-azikugwadirani kapena aziti wee bambo! mukamamuitana? Ulemu wake uti? Nkhanitu mukapanda kuilongosola inuyo bwinobwino kumakhalanso kovuta kuti munthu akuthandizeni zenizeni chifukwa simunaitambasule. Nditengerepo mwawi wopempha ena amene ali ndi mavuto ndipo akufuna kuti ndiwathandize kuti aziyala nkhani yawo bwinobwino, momveka kuti ndithe kumvetsa gwero la vuto lawo ndipo ndikatero nditha kupereka malangizo malinga ndi nkhani yawo mmene ilili. OFUNA MABANJA Ndine wa zaka 37 ndikufuna mkazi wa zaka kuyambira pa 40 mpaka 45. Wosangalatsidwa aimbe pa 0888 512 430 Ndili ndi zaka 27 ndipo ndikufuna mkazi woti ndipange naye chibwenzi ncholinga choti tidzakwatirane mtsogolomu. Akhale wa zaka za pakati pa 18-23, koma akhale wa ku Lilongwe. +Ndine mnyamata wa zaka 30 ndikufuna mkazi wa zaka za pakati pa 30 ndi 33 kuti ndipalane naye chibwenzi. Wotsimikiza aimbe pa 0888 904 690 kapena pa 0998 707 410. +Ku Machinga akonzekera ulimi wa fodya Alimi a mmakalabu 7 ati chaka chino akonzeka kulima fodya wochuluka ncholinga chosintha mabanja awo pachuma popeza iwo amakhulupirira kuti fodya ndi mbewu yomwe imabweretsa chuma chochuluka pakhomo. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Nkhaniyi idadziwika pamene Kampani ya Japanese Tobacco International (JTI) sabata yatha idapereka feteleza pangongole kwa alimi ochokera mdera la mfumu Ngokwe mboma la Machinga pamwambo womwe udachitikira pamsika wa Ngokwe ndipo alimiwo adatsindika kudzipereka paulimiwu chaka chino kuti Malawi asimbe lokoma ndi ndalama zakunja zomwe zimathandizira kuyendetsa ntchito za chitukuko mdziko. +JTI idaganiza zochita machawi pofuna kuwagwira mkono alimiwo kuti akwaniritse masomphenya awo. +Kampaniyo idakongoza alimiwo matumba a feteleza okulitsa a Super D Compound kwa onse omwe adapanga makalabu a zaulimi kuti iwo alime fodya wochuluka ndi kumusamala bwino. +Mmodzi mwa alimiwo, Sitola Banda, adati JTI ikuthandiza alimi a mbomalo kukwaniritsa malingaliro awo kuti chaka chamawa boma lipeze fodya wochuluka. +Talandira ngongole ya matumba a feteleza wokulitsa ndipo tikukhulupirira kuti tigwiritsa ntchito thandizoli moyenera. Makalabu omwe ndi aakuluakulu adakongozedwa feteleza matumba 200 pofuna kuti achilimike ndi ntchito za kuminda yawo. Si bwino mlimi kusiya ntchito za kumunda nkumapita uku ndi uku koyangana feteleza mnyengo yoti ulimi wafika kale pampondachimera, Banda adatero. +Iye adati dera la Ngokwe makedzana lidali ndi minda ya fodya yochuluka ndipo alimi ankatumiza fodya wambiri kumisika ya fodya mdziko muno. Choncho iye adapempha alimiwo kuti adzipereke kotheratu kaamba koti nalonso boma limaika chidwi pafodya kuti chuma chiyende bwino. +Tiyeni titukule dziko lathu potenga nawo mbali paulimiwu. Mlimi wochenjera adafesa kale fodya wake kunazare ndipo pakadalipano maso ali tcheru kuyembekeza kumwamba kuti mvula igwa liti, adaonjezera Banda. +Mlimiyu, yemwe amachokera mkalabu ya Kondwerani mmudzi mwa Muwawa, T/A Ngokwe, adathokoza kampani ya JTI kaamba kowapatsa poyambira, zomwe zakhazikitsa pansi mitima ya alimi mderalo. +Tikuthokoza JTI popereka ngongole yochuluka chotere, apatu sitijejemajejema mvula ikayamba kugwa. Talandira matumba a feteleza okulitsa motengera muyezo wa fodya yemwe tidasayinirana kudzagulitsa kukampaniyo ndipo tikuyembekezanso kulandira matumba ena a feteleza wobereketsa posachedwapa, adatero Banda. +Tingopempha Chauta kutipatsa mvula yokwanira chaka chino kuti tikwaniritse khumbo lathu potukula mabanja ndi dziko lathu. Tikuyamikiranso kampaniyi popeza ikutilimbikitsa kubzala mitengo yambiri mmalo momwe tadulamo mitengo yogwiritsira ntchito paulimiwu kuti tichepetse kuononga chilengedwe kuderali, adaonjezera motero Banda. +Palinso mabungwe ena monga Mardef, omwe akuthandiza alimi kuderalo powapatsa ngongole ya zipangizo za ulimi kuti asasowe pogwira pamene ntchito ya kumunda yayambika. makedzana lidali ndi minda ya fodya yochuluka ndipo alimi ankatumiza fodya wambiri kumisika ya fodya mdziko muno. Choncho iye adapempha alimiwo kuti adzipereke kotheratu kaamba koti nalonso boma limaika chidwi pafodya kuti chuma chiyende bwino .Tiyeni titukule dziko lathu potenga nawo mbali paulimiwu, adaonjezera Banda. +Mlimiyu, yemwe amachokera mkalabu ya Kondwerani mmudzi mwa Muwawa, T/A Ngokwe, adathokoza kampani ya JTI kaamba kowapatsa poyambira, zomwe zakhazikitsa pansi mitima ya alimi mderalo. +Tikuthokoza JTI popereka ngongole yochuluka chotere, apatu sitijejemajejema mvula ikayamba kugwa. Talandira matumba a feteleza okulitsa motengera muyezo wa fodya yemwe tidasayinirana kudzagulitsa kukampaniyo ndipo tikuyembekezanso kulandira matumba ena a feteleza wobereketsa posachedwapa, adatero Banda. +Alandira upangiri pa malonda a mbewu Ochita bizinesi yogulitsa mbewu a mmaboma 7 mdziko muno alandira upangiri wa momwe angapewere kuononga bizinesi yawo popezeka ndi mbewu yachinyengo yomwe atambwali ena amakonza mwa iwo okha. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mchitidwe wopanga mbewu zachinyengo ukukula mdziko muno poti pakadalibe lamulo loletsa munthu kuyamba kukonza ndi kugulitsa mbewu, koma chodandaulitsa nchakuti atambwali ena amapanga mbewu yabodza nkuika mmapaketi a makampani odziwika kuti azinamiza anthu. +Apolisi ku Limbe agwirapo kale akamberembere ena omwe akugulitsa mbewu yachinyengo monga iyi Mmodzi mwa ogulitsa mbewu, Ashraf Botha, yemwe ndi mwini wake wa Jumark Investments mboma la Machinga, adapereka umboni kuti adalandirako mbewu yachinyengo poyesa kuti ndi mbewu yomwe amagulitsa chaka chilichonse. +Iye adati adadzidzimuka kuona kuti alimi ambiri omwe amamugula mbewu ndi zipangizo zina zaulimi, chaka chino akubwera ndi madandaulo kuti mbewu yawo sikumera ndipo izi akuti zidachititsa kuti iye agule mbewu ina nkupereka kwa alimiwo mwaulere. +Alimiwo ndi makasitomala anga ndiye ndidangololera kuti ndiluze ndine ndipo ndidagula mbewu ina kukampani ina nkuwapatsa ndipo akuti idamera, koma ndikukambirana ndi eni kampani yoyamba aja kuti andithandiza bwanji, adatero Botha. +Potsatira malipoti akuti anthu ena agwidwapo kale ndi mbewu yachinyengo, bungwe la International Maize and Wheat Improvement Centre (CIMMYT) lidachititsa maphunziro a ogulitsa mbewu kuwaphunzitsa momwe angazindikirire ngati mbewu ili yeniyeni ndi momwe angathandizire alimi kupewa kupusitsidwa. +Msonkhanowu udachitikira mumzinda wa Lilongwe Lachisanu lapitali ndipo oyanganira ntchito za bungweli, Willie Kalumula, adati cholinga cha maphunzirowo nchakuti ogulitsa mbewu azitha kuzindikira mbewu yachilungamo ndi yachinyengo komanso azikhala ndi upangiri wokwanira woti akhoza kuunikira alimi. +Sitikufuna msika wa mbewu woti bola ndagulitsa, ayi, koma ogulitsa azikhala ndi upangiri ndipo azitha kuunikira alimi pa za mbewu zomwe angabzale mmadera mwawo komanso kuti azitha kuzindikira mbewu yachilungamo ndi yachinyengo, adatero Kalumula. +Mmodzi mwa anthu omwe adachita nawo maphunzirowo, Jessie Mazengela, yemwe ndi mwini wake wa Zilimnthaka Investments kwa Mkanda ku Mchinji, adati maphunzirowo adawatsegula mmaso powaunikira kuti ndi bwino kudziwa mbewu zomwe akugulitsa. +Za maukwati, mabanja Money is gooooood Musayense njerego, awa ndi mawu ochokera munyimbo ya Miracle Money ya mnyamata wodziwa kuimba nyimbo zauzimu, Onesmus. Poyamba, ndinkamva ngati akuti God is good! Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Iyitu ndi nyimbo yauzimu imene imakamba za ndalama zozizwitsa zimene zingapezeke mkachikwama kanu kapena kubanki modabwitsa. Akhoza kukhala mamiliyoni. Si za kashigetitu! Major do it! Major do it! Pamenepanso ndimayesa akuti God do it! God do it! Zoona, ambiri timalambira dzuwa mmalo molambira wolenga dzuwalo. +Musayambe kundinena kuti ine zindikhudza bwanji. Inetu ndimakhulupirira kwambiri Mateyu 7 vesi ya 1: Osaweruza ena chifukwa ndi mlingo umene uweruzira ena, nawenso udzaweruzidwa. Ndine ndani ine, kapunthabuye, kafucheche, kwakwananda ndipo ndikadakhala nsalu bwenzi ndili kilimpulini. +Sindinakumalizireni nkhani ija sabata yatha. Tidaika zovuta kumanda ena pafupi ndi pa Wenela. Ubwino wake, wotisiyayo adali atagula kale puloti yake kumasanoko. +Titaika zovutazo, mkulu wina adanditengera pambali: Tade kodi panthumbira paja anaikapo maluwa chifukwa chiyani? Kodi malemuwo adali kalipentala? Nanganso anaikapo mtanda wa thabwa, kodi malemuwo adali kalipentala? Sindikaika kutsogoloku adzawaka mandawo ndi simenti ndi quary ngati malemuyo anali kontilakita. +Sindidamuyankhe. +Titafika malo aja timakonda pa Wenela, kudatulukira mkulu wina atanyamula zibonga ndi mikondo. +Tiwaphe basi! Amenewa aphedwe basi! Ndithu pa filling station munthu angathire mafuta kotulukira utsi? adafunsa mkulu wa zikwanjeyo. +Dzina lake ndi Nike Masonda, mnzake wa Adona Hilida ku Polisi Palibe. Tsono akadati alowe kumpanda ku Sanjika bwenzi ataika malamulo wotani mkuluyo? Zidandipita. +Koma Abiti Patuma akuoneka kuti adazitolera. Pezani zina zokamba. Ndimayesa muzinena za chimbudzi choyendayenda cha Moya Pete. Zomwe mukunenazo tidazimva kale. Ati Mugabe adawauza akwatirane ndipo mubadwe mwana, apo ayi awakhiya pakhosi, adatero. +Ndipo izo zili apo, tidamvaponso za wina amene ankanena kuti satana akadakhala wa maganizo otere bwenzi atapusitsa Adam osati Hava kuti adye chipatso cha pakati pamunda. Koma zochitika kuchipinda kwa wina inu zimakukhudzani chiyani? adafunsa Abiti Patuma. +Mkulu uja adati: Musathe mpweya, malamulo amaletsa kuchita zosayenerazi. Ngakhale malembo oyera amaneneratu. +Malamulowo amaneneratu kuti si bwino kugonana motsutsana ndi chilengedwe. Titati tilowe mzipinda mwa inu mukudzitcha olungama sitikapeza mukuphwanya lamulo? adaphaphalitsa funso Abiti Patuma. +Abale anzanga, mwinatu mukufuna kumva maganizo anga pankhaniyi. Ndine mmodzi mwa anthu amene amakhulupirira kuti ngakhale nyerere zimadziwana kuti iyi ndi yaimuna, iyo yaikazi, chimodzimodzi agalu, abakha, nguluwe ndi akamba. Chinanso nchakuti tikadati tonse tiziganiza chomwechi, bwenzi dziko ndi anthu ake alipo? Koma mbali inayi, zochitika kuchipinda kwa ena ine sizindikhudza; ndilibe nazo ntchito. Pamene ena akuchita kusaweruzika ine sindikhala nazo ntchito. +Zonse zili apo, ndimakhulupirira kuti chilengedwe chiyenera kutsatidwa basi. Ndimaopa kuti zipata zitatsegulidwa, mwana wanga Zeno akhoza kuona ngati kukhalira limodzi atambala okhaokha palibe chachilendo. +Anatchezera Sitinakumanepo Anatchereza, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndili ndi mkazi amene ndidamufunsira pafoni koma sitinaonanepo. Timangoimbirana foni basi koma amandiuza kuti amandikonda kwambiri. Ndimukhululupirire? Zikomo, Nzovuta kukuthandizani chifukwa simunanene kuti zidayamba bwanji kuti mumufunsire mkaziyo pafoni. Kodi nambala yake mudaitenga kuti? Adakupatsani ndi mbale wanu kapena mbale wamkaziyo? Mnzanu? Mnzake? Mwa njira iliyonse, nanunso mukuonetsa kuti mukhoza kukhala ndi kamtima ka chisembwere kapena mwalifunitsitsa banja ndiye mukufuna kupeza mkazi basi. Dekhani. +Komanso ine pokhala wa mvula zakale zambiri zikumandidutsa komabe adzukulu ena amandiuza kuti kunjaku kwadza njira zamakono zochezera pafoni monga Whatsapp, Facebook ndi zina zotere. +Sindikudziwa ngati nkotheka kuti mudapatsana manambala kupyolera mnjira zimenezi. +Choti mudziwe nchakuti njira zopezera mwamuna zimakhala zosiyanasiyana koma chachikulu chimakhala chakuti munthu amene ukumanga naye banja ayenera kukhala yekhayo ukumudziwa bwino. +Pali banja apa? Zikomo gogo, Tidamangitsa ukwati ndi mkazi mu 2010. Tili ndi mwana mmodzi. Ali ndi mimba, iye ankakana kukhalira malo amodzi ati poopa kuti mimba ichoka. Nkhaniyo ndidaitengera kwa ankhoswe omwe adatithandiza kuti ziyambenso kuyenda monga banja. Koma mwanayo atabadwa, iye adayambanso kukana zokhalira malo amodzi ati chifukwa azikhala wotopa. +Nditayitengera nkhaniyo kwa ankhoswe, adayikanika. +Kuntchito adandisamutsira ku Mzuzu koma iye adakana kupita nawo. Ndidapitiriza kumulipirira lendi koma patatha miyezi ingapo adachoka ndipo adapita kwa mayi ake ku Blantyre. +Ndidapita komweko koma ukunso adakana zoti tikhalire malo amodzi. Ndichitenji? NJ, Zomba. +NJ, Ndikudziwa kuti kukhalira pamodzi si ngodya yokhayo yomangira banja koma iyi ndi njira yosonyezera chikondi pa mwamuna ndi makzi wake choncho ngati wina apezeka kuti akulanga mnzake mnjira yotere, zimasonyeza kuti penapake zinthu si zili bwino. +Zifukwa zimene mkazi wanuyo akupereka ndi zopanda pake, kusonyeza kuti pali china chimene akubisa. Msinkhu wangawu, sindidamvepo kuti mimba yachoka chifukwa mwamuna ndi mkazi amagonana mkaziyo ali woyembekezera ndiye izi akuzitenga kuti? Komanso mudziwe kuti mkazi wanuyo akudziwa kuti apa banja lathapo basi. Poyamba, kukukanizaniko. Kachiwiri, nchifukwa chiyani adakana kukutsatirani kuntchito? Ndipo pomaliza nchifukwa chiyani wabwerera pakhomo la amake? Zonsezo ndi zizindikiro kuti apa paipa. +Chofunika nchakuti mupite kwa ankhoswe mukatule nkhaniyi. +Adasintha Gogo, Ndili ndi mkazi yemwe ndili naye mwana wa zaka zitatu. Malinga ndi mavuto a zachuma, ndidachoka ku Blantyre kudzagwira ntchito ku Lilongwe. Patatha miyezi ingapo adanditsatira. +Koma chongobwera kuno, iye adasintha ndipo amakonda kucheza ndi amayi oyendayenda. +Ndichitenji? M, Lilongwe. +M, Poyamba simunandiuze ngati ukwati wanu uli wa kwa ankhoswe kapena mudangotengana. Ngati ndi wa ankhoswe, kawakambireni. +Ngati ayi, poyamba muyenera kumufunsa mkazi wanu chifukwa chimene akuyendera ndi amayi oyendayendawo. Mumuuze kuti ayenera kusintha ndipo ngati sasintha, chochita mukuchidziwa kale. Kunjaku kwaopsa adzakubweretserani matenda. +Chithunzithunzi cha gogo wathu Mukunyasitsa nkhope mwayambana ndi ndani Munthu wokwiya saoneka bwino Amakhala ngati mtembvo omwe ukanka kumanda Maliro ake ochita kupha ndi mwala Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Iyi ndi nyimbo ya Phungu Joseph Nkasa imene inkaphulika malo aja timakonda pa Wenela tsiku limenelo. +Kuchipululu Kalekalelo, anasankha wolakwika Waumphawi, ndi umbuli Anasankha wolakwika Koma Gervazzio! Sindidziwa kuti amaganiza chiyani posankha nyimbo. +Posakhalitsa idatulukira basi. Adatulukamo Moya Pete, tsinya lili kuno! Mumandinena kwambiri, kuti ndinatenga mbuzi 200 kupita kukaonana ndi Bani Kimwezi wa Nations Unie. Nonsense! Nonsense! Mulibe nzeru nonse, kodi simudziwa ndili nawo ochuluka makobidi? Kafunseni mabanki a ku Switzerland! Izi ndi zangazanga ndalama. Nkati ndikuuzeni, pamwezi ndimalandira K1 400 ndiye mukati ndimayenda kuti ndizidya ndalama zanu. Nonsense! adatero tisanamupatse moni. +Pomwepo, adayamba kukwapula basiyo mokwiya. +Nonsense kwambiri. Sindidya pakhomo panu. Ndikapita ndi mbuzi 601 dziko lija la Amerigo Vesipusi mwati ndalakwa? Kodi enatu anabwera masauzande! adazaza Moya Pete. +Inetu ndimadabwa kuti munthu akangolawa zamchere ndithu amapenga ngati mbuzi! Abiti Patuma amaganizanso chimodzimodzi. +Akulu, khazikitsani mtima pansi. Sikuti mukamalankhula ndi mkwiyo ndiye kuti mukunena zoona. Ndipo enafe timaona kuti munthu akamakalipa, kutenga aliyense ngati chidzukulu chake, timadziwa kuti pali chimene akubisa. Timakumbukatu za Adona Hilida, Mpando Wamkulu ngakhalenso uyu mwati ndani uyu. Mfumu Mose, adatero Abiti Patuma. +Abale anzanga, chiwanda choyenda ndi mapazi ichi. +Ndakwiya kwambiri. Ndikhozanso kuzisiya kwambiri! Kodi mwaiwala kuti gogo uja naye ankakwera ndege monga enanu muchitira kabaza? Bwanji simunkamutsutsa? Ine ndikangoti ndilaweko kabaza wa ndegeyu mwati mfwemfwemfwe! Nonsense! adatero Moya Pete, uku akunyamula tambula ya madzi ozizira. +Adamwa. Adanyambitira. Adatafunira ngati mmadzimo mudali nsenga. +Gogo amanenedwa apatu ndi uja adandipeza ndikulima osavala ndili kwathu kwa Kanduku. Inde, gogo yemwe uja adapita uku ndi uko kukanena kuti adandipeza ndili buno bwamuswe! Mwaiwalatu china chake akulu. Gogo mukunenayo ulamuliro wake udali wayekhayekha ndipo padalibe omutsutsa. Ifetu tikamakutsutsani timakufunirani zabwino, adatero Gervazzio. +Ana osakhwima paliombo. Mwaiwala kale zazikulu zimene ndakuchitirani? Munali yani, anthu oipa mwapanga bwanji? adafunsa Moya Pete. +Palibe adayankha. Aliyense adafa nalo phwete. +Tsoka lake, mukakhala kuchipinda kwanuko, kudikira kumwa wamkaka tiyi mumaona ngati zonse zikuyenda. Kodi inuyo a Dizilo Petulo Palibe mudawauza anthu kuti mudzathana ndi zoti tizichita Jump Carefully? Nanga zolipira kundagala mudanenapo? Taipa lero? adatero Abiti Patuma. +Abale anzanga, palibe icho ndidatolapo. +Mwambo wa ufumu pakati pa Achewa Ufumu ndi udindo wa utsogoleri womwe umalira munthu waluntha ndi wakhama komanso wachikondi ndi wachilungamo kuti mudzi mtundu usasokonekere komanso pakhale chilungamo ndi mtendere. Wapampando wa gulu la Achewa la Chewa Heritage Foundation (Chefo) Professor George Kanyama Phiri akufotokozera STEVEN PEMBAMOYO momwe mwambo wa ufumu umayendera pakati pa Achewa. +Kanyama: Amayi amatenga gawo lalikulu Ndikudziweni. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ndine Professor George Kanyama Phiri ndipo ndine wapampando wa gulu la Achewa la Chewa Heritage Foundation (Chefo) muno mmalawi udindo omwe ndidaulandila kuchoka kwa a Justin Malewezi. +Poyamba tandiuzani za utsogoleriwu kuti umayenda bwanji. +Utsogoleri wa gulu limeneli umasiyana ndi utsogoeri wa magulu kapena mabungwe ena chifukwa siutengera chisankho ayi koma mwini wake mfumu ya Achewa Kalonga Gawa Undi amachita kusankha akaona kuti wina watsogolerapo ndipo wakhutira naye. +Chabwino nkhani ili pano ndi ufumu pakati pa Achewa. Kodi ufufmuwo umayenda bwanji? Ufumu wa Achewa umayendera kwa amayi kusiyana ndi mitundu ina yomwe imatengera abambo. Mfumu ikakalamba kapena kumwalira, amaona kuti kodi kumakolo ake kuchokera kwa azimayi angavale ufumuwo ndani. Amayambira ku banja lalikulu nkumatsika mpaka atapezeka olowa ufumuwo. +Amasankha ndani ndipo amasankha bwanji? Amasankha ndi amayi a kubanja la chifumulo. Mfumu ikakalamba, amayi amakhala pansi nkuunika kuti angadzalowe mmalo ndani ndipo akapezeka amauza madoda (abambo) omwe amaitanitsa mlowammaloyo nkupanga zoti aziyenda ndi mfumuyo kulikonse kuti aziphunzirako zina ndi zina. Chimodzimodzi mfumu ikamwalira, msangamsanga azimayi amakhala pansi nkusankha mlowammalo. +Nanga bwanji pamapezeka kuti ena akulimbirana ufumu mpakana kubwalo lamilandu? Pamwambo wa Chichewa kumene kuja nkulakwitsa chifukwa ndondomeko ilipo kale ndipo ndiyokhazikika yongoyenera kutsatidwa. Mpata woyamba kubanja la amayi aakulu kenako owatsatira kukamalizira kumunsi mpaka mlowammalo atapezeka. Zimatheka kuti amayi akuluakulu onse osasankhako mfumu chifukwa pali zomwe azimayiwo amaona posankha. +Zinthu monga ziti? Zilipo zambiri monga khalidwe la munthu, chilungamo, maonekedwe chifukwa mfumu imafunika izikhala yolemekezeka mmaso kuti ikalankhula kapena kugamula mlandu anthu aziti apa pagamulidwa mlandu osati kumaderera. Mfumu amafunikanso kukhala wachilungamo, opanda ziphuphu, odziwa kugawa, wachikondi ndiwolimbika pochita zinthu kuti anthu ake azimutsatira. +Ndiye akasankha dzinalo chimachitika nchiyani? Amayi akasankha dzina la mfumu, amakapereka dzinalo kwa abambo omwe amapitiriza zina zonse monga kutumiza mauthenga kwa mafumu ena komanso kuofesi ya DC ndi kukonza tsiku la mwambo oveka ufumu. Muyenera kudziwa kuti ufumu wa Chichewa amaveka ndi mafumu akwina osati eni ake ayi ndiye mafumu oterowo amayenera kulandira uthenga nthawi yabwino. +Ntchito ina ya amayi ndi chiyani pamwambo wolonga mfumu? Mwachidziwikile azimayi ndiwo amakonza zakudya ndi zakumwa pamwambo koma kupatula apo, amakhalanso ndi ntchito yokonza anamwali chifukwa pamwambo wa ufumu, Achewa amatengerapo mpata wolanga anamwali. Uwu uli ngati ulemu wapadera wa mafumu komanso amayi amathandiza kwambiri kumbali ya magule okometsela mwambo. +Nanga pamwambopo pamakhala zotani? Pamwambo wa ufumu wa Achewa pamakhala magule amakolo, pamakhalanso kufotokoza mbiri ya ufumu omwe ukuvekedwawo kenako bwanamkubwa amawerenga malamulo a kayendetsedwe ka ufumu nkuveka olowa ufumuwo mkanjo wa ufumu kwinako magule ndi madyelero amapitirira. +Kutumiza ana kundende si yankhoJaji Jaji wa kubwalo lalikulu (High Court) Justice Annabel Mtalimanja wati kuthamangira kugamula ana achichepere kukagwira ukaidi kundende ndi njira imodzi yopititsira uchigawenga patsogolo. +Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Mtalimanja adalakhula izi posachedwapa poyamikira ntchito yomwe likugwira bungwe losamala ana ndi kuwaphunzitsa zachikhalidwe chabwino la Chisomo Childrens Club. +Mtalimanja: Ana asapite kundende za akulu Mtalimanja adati ana achichepere akapita kundende amakakumanako ndi anamandwa pazauchigawenga omwe amawagawira nzeru zolakwika ndipo akatuluka amakayeserera zomwe adaphunzirazo moyo wauchigawenga nkupitirira. +Nkoyenera kwake kuti munthu yemwe walakwira lamulo alandire chilango koma mpofunika kuunika bwino kuti kodi chilango chomwe chikuperekedwacho zotsatira zake zikhala zotani chifukwa cholinga cha chilango nkuwongola, koma nthawi zina kumatheka kukhotetserakhotetsera. +Chomwe ndikutanthauza apa nchakuti chilango chomwe chikuperekedwa chizifanana ndi msinkhu wa munthu wolangidwayo. Ana achichepere, mwachitsanzo, akhoza kuongoka polandira maphunziro achikhalidwe chabwino, adatero Mtalimanja. +Bungwe la Chisomo Childrens Club lidayambitsa pologalamu ya Mwayi Wosinthika yomwe amaphunzitsa achinyamata opezeka olakwa za mmene angasinthire moyo wawo ndi kukhala achinyamata odalirika. +Mkulu wa bungweli Charles Gwengwe adati pakalipano bungweli laphunzitsapo achinyamata ochuluka ndipo pano ena adasinthiratu moti akugwira ntchito, ena akuchita bizinesi ndipo ena adabwerera kusukulu. +Sitiphunzitsa zakusukulu, ayi koma mmene munthu angakhalire ngati munthu pakati pa anzake. Ambiri mwa ana omwe timaphunzitsa amakhala ndi milandu ingonoingono monga kupezeka malo olakwika ngati omwera mowa, kuchita mchitidwe woyendayenda ndi kuba pakhomo pa makolo awo. +Timayenda mmalo oweruzira milandu, mndende, ndi kupolisi kusakasaka ana a milanduyi ndipo tikawapeza timapanga dongosolo lowatenga kuti tikawaongole, adatero Gwengwe. +Pologalamuyi imayenda ndi thandizo lochokera ku Ireland kudzera mu nthambi yolimbikitsa njira zina za kaweruzidwe ka milandu yomwe imatchedwa kuti mpatutso (Diversion Program). +anatchezera Akunyengana ndi mnzanga Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Zikomo Anatchereza, Ndakhala pabanja zaka 7 ndipo tilinso ndi mwana wa zaka 7. Tsiku lina mwanayo adathyoka mkono ndipo adatigoneka kuchipatala sabata ziwiri ndi masiku 4. +Ndili konko, ndidamva kuti mwamuna wanga akuyenda ndi mnzanga, yemwenso ndi woyandikana naye nyumba. Titatuluka adabwera kudzandiuza kuti mwamuna wanga adamufunsira koma adawakana. +Nditawafunsa amuna anga adakana. Chodabwitsa nchakuti, usiku mwamuna wanga amasowa. Kuyangana kuchimbudzi, kubafa ngakhalenso pakhonde osaoneka. +Ntawapanikiza, adaulula kuti amayendadi ndi mnzangayo. Powafunsa ngati ndili ndi vuto adati palibe, koma Satana ndiye adawanyenga. Ndichitenji? EKM EKM, Amuna anuwo alibee chikondi chenicheni. Iwowo povomereza kuti amanyengana ndi mnzanu, aonetseratu ukamberembere wawo. Poyamba ndi kukana ndiye kusowa chikondiko. +Chokaikitsa china nchakuti mnzanuyo adabwera yekha kudzakuuzani kuti amuna anu adamufunsira koma adanama kuti adawakana. Ichi chidali chiphimba mmaso chabe chifukwa amadziwa kuti manongonongo a uhule wake akufikani. +Zikatere nkutani? Kunjaku kudaopsa ndipo si bwino kusekerera mwamuna kapena mkazi wosakhulupirika. Nthawi yoimbs nyimbo ya kapirire kunka iweko idatha. +Kaitureni nkhaniyi kwa ankhoswe chifukwa uwu ndi mlandu wachigololo choletsedwa ndi Ambuye. +Apachibale akundifuna Anatchereza, Pali anyamata awiri a pachibale amene akuoneka kuti amandifuna. Mmodzi mwa anyamatawo ndidamudziwa kalekale ndipo wakhala akundifundira koma ndimamukana. +Ndidadziwana ndi winayo chifukwa cha mbale wakeyo ndipo nsye akunditumizira mauthenga a chikondi, ati akundifuna. Ndichitenji, chifukwatu awiriwo akundisowetsa mtendere. +M.E. +Mponela ME, Ngati anyamatawo simukuwafunadi ndi bwino kuwauziratu, mmalo mowapatsa banga kuti aziganiza kuti mwayi ukadalipo. +Mwinatu inuyo simutsindika kukana kwanuko. Komanso nkutheka kuti anyamatawo ndi nkhakamira. Mwinanso ali pampikisano kuti aone angakutengeni ndani. +Muli monsemo, mphamvu zili mmanja mwanu, kulola kapena kukana. +Ana owapeza avuta Zikomo Anatchereza, Ndakhala pachibwenzi ndi mkazi wina yemwe ndidalowa naye mbanja chaka chatha. Iye adabwera ndi ana ake awiri ndi abale ena ndipo polingalira kuti ndi banja, nanenso ndidakatenga mwana wanga. +Iye akungokhalira kulalatira mwana wangayo ati ndi wamwano. Nthawi zina akumachita izi panja kuti a nyumba zoyandikira amve. Akuti ngakhale nditachoka sangadandaule, chonsecho ali ndi pathupi pa miyezi 7. +Ndapirira mokwanira, ndithandizeni. +WL, Lilongwe. +WL, Musanachite chilichonse pabanja mumayenera kukambirana kaye. Momwe zikuonekera apa, mkazi wanuyo adakangotenga ana ndi abale akewo musanakambirane. Nanunso mudangoyendera yanu nkukatenga mwana wanu. +Choncho kusamvana sikungalephere kubwerapo. +Komatu apa palibe chifukwa chokwanira choti nkuthetsera banja. +Khalani pansi nkumanga mfundo imodzi. Ndi ana ndi abale ati amene ayenera kuchoka pakhomopo ndipo ndi angati amene ayenera kuchoka? Mukuyembekezera mwana wanu, kusonyeza kuti udindo wanu ukukula. Anatchereza Ndimutsatirebe? Ine ndidakwatiwa ndi mwamuna wa ku Zimbabwe ndipo takhala limodzi mpaka mu 2012 pomwe adachoka kupita ku Joni. Ndili naye mwana mmodzi. Poyamba ankatumiza chithandizo ndipo timaimbirana foni koma pano olo foni saimba, chithandizonso adasiya kutumiza. Koma adandipangitsira pasipoti kuti ndimtsatire ku Joniko koma abale ake adayankhula mwathamo kuti adakwatira ku Joni komweko. Ndiye nditani pamenepa, ndikwatibwe kapena ndizidikirabe? Nditani ine, gogo wanga, poti ndidakali wachitsikana? EE, Blantyre Wokondeka EE, Ndamva nkhawa zako ndipo ndakhudzidwa kwabasi ndi mmene ukwati wako ndi mwamuna wa ku Zimbabweyo ukuyendera. Koma nanenso ndili ndi funso kuti ndithe kukuthandiza bwino. Kodi ukwati wanuwo ndi womanga bwinobwino ndipo ndi wovomerezeka ndi mbali zonse ziwiri za kuchimuna ndi kuchikazi? Ndatero chifukwa pakuoneka kuti ukwati wanu ulibe ankhoswe nchifukwa chake abale ake a mwamunayo akukuyankha mwathamo kuti uiwaleko za iye ati chifukwa adakwatira mkazi wina ku Joniko. Maukwati ambiri akhala asakulongosoka chifukwa achinyamata masiku ano amakonda madulira, osafuna kutsata ndondomeko zonse zofunikira asanalowe mbanja. Mnyamata akangoti I love you basi msungwana khosi gonekere kenaka wakamulowerera mnyumba ali basi takwatirana. Posakhalitsa mavuto otere amayamba mbanja lotereli, zinthu osalongosokanso. Tsono apa, mwana wanga, chimene ndikuona nchakuti mwamuna wakoyo walithawa banja nchifukwa chake chithandizo olo foni adasiya kukutumizira. Iwe ukamuimbira amakuyankha nanga? Ndikukaika. Likadakhala banja lenileni ndidakati upite kwa ankhoswe akuthandize, koma ndakaika ngati alipo. Ndiye chomwe ungachite apa nmumuiwala mwamunayo ndi kuyambiranso wani. Si wanena wekha kuti udakali mtsikana! Koma ulendo uno uyesetse kuti utsate ndondomeko zonse zimene zimayenera kutsatidwa munthu ukafuna kulowa mbanjaiwe ndi bwenzi lako mudziwane bwinobwino ndipo lidzaonekere kwanu ndi akwawo kudzatomera ukwati; pakhale chinkhoswe cholongosoka; kenaka ukwati wololedwa. +Wezzie: Chiphadzuwa chonenepa cha Mzuni Sukulu yaukachenjede ya Mzuzu University idasankha chiphadzuwa chonenepa Loweruka sabata yatha pomwe adali ndi chisangalalo chawo cha Social Weekend. Mtolankani wathu DAILES BANDA adacheza naye motere: Tikudziweni Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Ndine Wezzie Lwara ndipo ndimachokera mmudzi mwa Thom Lwara, kwa Inkosi ya Makhosi Mmbelwa mboma la Mzimba. Kwathu tinabadwa ana awiri ndipo ndine woyamba kubadwa. Ndili ndi zaka 20. +Manthu wa ziphadzuwa: Lwara (pakati) ndi omutsatira ake Mbiri yako ya maphunziro ndi yotani? Ndidalemba mayeso anga a Fomu 4 pasukulu ya sekondale ya Ekwendeni, padakalipano ndikuphunzira zokopa alendo pa Mzuzu University. Ndili chaka chachiwiri. +Udayamba liti za uchiphadzuwa? Kunena chilungamo aka nkoyamba kuchita izi. Mnzanga wina adangobwera kudzandiuza kuti ndikayese ndipo ndikhoza kupambana. Kuyesera ndi kupambana kudali komweko. +Udazilandira bwanji za kupambana kwako? Sindikuchitenga chinthu chapafupi chifukwa sindidakonzekera kwambiri monga anzanga adachitira. Ndine wosanglala kwambiri makamaka chifukwa cha mphatso yomwe ndidalandira ya ndalama zokwana K50 000. +Ndiye ukuwauza chiyani makolo ako? Kusukulu ya ukachenjede ndi komwe anthu amaphunzira ndi kuchita zinthu za msangulutso zambiri. Iyi ndi nthawi yomwe aliyense amene adapitako kusukuluzi amakumbikira kuti adasangalala. +Atsikana uwalangiza zotani? Azilimbikira sukulu kuti adzafike malo ngati ano ndipo asamakhale ndi mtima odziderera. Pa atsikana amene tidapikisana, sikuti pasukulu pano atsikana onenepa ndife tokha ayi koma kumakhala kudzikaikira komwe kumatilepheretsa kuchita zinthu. +Si zonyengerera mu 2016Mkulu wa polisi Anthu ali kalikiriki kukonza mapulani a chaka chatsopano cha 2016 koma ngati mapulani ake akukhudza umbanda ndi ziphuphu, dziko lake si lino, waneneratu mkulu wa Polisi mdziko muno, Lexten Kachama. +Kachama adalankhula izi pa 31 December 2015 pomwe apolisi amakondwerera chaka chatsopano kulikulu la polisi ku Area 30 mumzinda wa Lilongwe. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Lexten Kachama Chaka cha 2016 chikhala chaka cha chitsanzo pankhani yolimbana ndi mchitidwe wa uchifwamba, umbanda ndi ziphuphu. Tithana ndi zigawenga zonse komanso onse omwe akufuna kulemera kudzera mziphuphu, adatero Kachama. +Iye adati mchaka cha 2015, apolisi adayesetsa kulimbana ndi mchitidwe wa uchigawenga ndi umbanda koma ngozi za pamsewu zidakwera ndi 18 pangozi 100 zilizonse kuyerekeza ndi mchaka cha 2014. +Kachama adati chimodzi mwa zifukwa zomwe zidachititsa izi ndi ziphuphu zomwe apolisi ena apamsewu amalandira kuchokera kwa eni galimoto zosayenera kuyenda pamsewu. +Nkhani ya ziphuphu ndi imodzi mwa nkhani zomwe apolisi amatchuka nazo makamaka pamsewu. Komabe ndinene pano kuti si apolisi onse omwe amachita izi koma apolisi ochepa chabe adyera, adatero Kachama. +Iye adati chaka chino akhwimitsa chilango chomwe apolisi opezeka ndi mlandu wa ziphuphu amalandira ndipo adachenjezanso anthu omwe amakopa dala apolisi ndi ndalama kapena zinthu zina kuti awatsekere milandu yawo. +Malinga ndi kafukufuku wathu, wapolisi wongolembedwa kumene ntchito, maka amene ali ndi satifiketi ya fomu 4, amalandira ndalama zosaposera K50 000 asanaduleko msonkho. +Ndi mmene mitengo ya zinthu ilili panopa, nkosatheka kuti munthu akwaniritse zofunika pamoyo wake wa tsiku ndi tsiku ndi malipiro achepa ngati awa poganizira chakudya, nyumba ya lendi, fizi ya ana asukulu, zovala ndi zina zotero zofunika pamoyo wa munthu. +Mwina ichi nkukhala chimodzi mwa zifukwa zomwe mchitidwe wa katangale ndi ziphuphu watenga malo pakati pa apolisi. +Kachama adalonjeza kuti apolisi ayesetsa kugwira ntchito yokomera anthu koma adati kuti izi zitheke, anthu akuyenera kutengapo gawo makamaka potenga apolisi ngati abwenzi awo powatsina khutu akawona zodabwitsa mmadera momwe akukhala. +Pothirapo ndemanga, mkulu wa bungwe loona za maufulu a anthu la Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR), Timothy Mtambo, adati uthenga wa mkulu wa polisiyu wafika panthawi yoyenera pomwe malingaliro a zauchifwamba za mu 2015 akadali mmitima. +Iye adati mchaka changothachi, uchifwamba udakula mpaka apolisi kumaphedwa ndi zigawenga zomwe zimadetsa anthu nkhawa pazachitetezo cha moyo ndi katundu wawo. +Chitetezo ndiye gwero la chitukuko cha mtundu uliwonse. Mabizinesi, zipembedzo, ufulu wa anthu ngakhaleso zomangamanga zimayenda bwino pakakhala chitetezo chokwanira chifukwa anthu amapanga zinthu mtima uli mmalo, adatero Mtambo. +Iye adati pulani ya apolisiyi singatheke pokhapokha boma litaikapo mtima powapatsa zipangizo zokwanira zogwirira ntchito yawo komanso kuwaganizira pankhani ya umoyo ndi makhalidwe awo. +Mwa zina, Mtambo adati apolisi amasowa chilimbikitso kaamba kakuti malipiro omwe amalandira ndi ogwetsa mphwayi, zomwe zimawafoola nkhongono; nyumba zomwe amakhalamo nzosaoneka bwino; komanso amagwira ntchito popanda zodzitetezera. +Nthawi zina apolisi amalephera kupita kukagwira ntchito yawo kaamba kosowa mayendedwe chifukwa cha nkhani za mafuta komanso galimoto. Apolisi amapezeka kuti akugwira ntchito mmalo a zipolowe koma alibe zodzitetezera, choncho sangagwire ntchito momwe akadagwirira chifukwa nawo ndi anthu, amafuna kudziteteza, adatero Mtambo. +Kusamala anapiye a mikolongwe Amati nkhuku ndi dzira, kusonyeza kuti ngati susamala dzira ndiye kuti udzalandira nkhuku za matenda zomwe sizichedwa kufa. Komanso kupanda kusamalira bwino anapiye, akhonzanso kufa. Koma chisamaliro ichi nchotani? BOBBY KABANGO adakacheza ndi Rose Mphepo, mphunzitsi wa kusukulu ya ziweto ya Mikolongwe mboma la Chiradzulu. Adacheza motere: Tidziwane mayi Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndine Rose Mphepo. Ndine Assistant Hatchery Managerwachiwiri kwa woyanganira malo oswera nkhuku. Koma tikuopeni? Mphepo kuyanganira anapiye Tikufuna timve momwe tingasamalire anapiye a mikolongwe. Kuno tilibe nkhuku mtundu wake mikolongwe. Anthu amangoti nkhuku za mikolongwe, koma palibe mtundu wa mikolongwe. Nkhuku zimenezi ndi ma Black Austrolorp koma chifukwa zimachokera kuno, anthu amangoti mikolongwe. Ndikufotokozerani momwe timasamalira anapiye koma tipite kuofesi kwathuko. Tsono tidaika madzi amene mukaponde musadalowe kuofesiko, madzi amenewo ndi a mankhwala kuti musabweretse matenda kukholako. +Chisamaliro cha anapiye amtundu umenewu chimakhala chotani? Ngati ukufuna kuweta nkhuku zimenezi, choyamba samala mazira. Ndiye tili ndi khola ilo lomwe tikusungako nkhuku 300. Tambala mmodzi ali ndi misoti 10. Zimaikira komweko ndipo mmawa cha mma 10 koloko timakatolera mazira komanso madzulo cha mma 3 koloko. +Mazira amenewa amapita kuti? Tikatolera, timapita nawo ku hatchery. Iyi ndi nyumba yofungatilitsa mazira kuti anapiye atuluke. Koma tisadawaike mnyumbayi, timawaika mu Egg Chamber. Awa ndi malo amene timasankhira mazira. Timaikapo zongendawa amene amapha timajeremusi tomwe dzira latenga kuchokera kukhola kuja. Timawasungamo kwa sabata imodzi. Tikawatulutsa mmenemu ndiye timawaika moti akafungatilitsidwe. Dzira ndi chinthu cha moyo, ngati taliyika mu incubator lili ndi majelemusi, ndiye kuti anapiye adzabadwanso ndi matenda. Komanso panthawiyo timasankha mazira amene ali ndi mavuto monga amene ali angonoangono komanso osweka. +Fotokozani zomwe zimachitika mu incubator-mo. +Incubator yathu imalowa mazira 30 000 koma chifukwa cha mavuto ena, sitikwanitsa kuikamo mazira 30 000, mapeto ake timangoika momwe tapezera koma sabata iliyonse Lachiwiri timatulutsa anapiye 4 000. Mavuto enanso nkuti tilibe zakudya zokwanira zosamalira anapiye ngati achuluka. Tikawaika mmenemu, timadikira padutse masiku 18, apa timasankha mazira amene satulutsa anapiye. Dziwani kuti tambala akaphonya pamene akukwera thadzi, dzira limenelo limakhala lakufa loti simutuluka napiye. +Zimakhala bwanji kuti Lachinayi lililonse muzitulutsa anapiye? Nchifukwa choti sitiika mazira 30 000 monga ilili incubator-yi. Ndiye sabata ino timaikamo mazira, ena timaika sabata yotsatira, zomwe zimachititsa kuti anapiye azitulukanso mosiyana. Ena amatha masiku 21 sabata ino pamene ena sabata ya mawa. +Kodi anapiye sangapse mmenemu atati atuluka chifukwa cha kutentha? Kutentha kwa incubator ndi kofanana ndi nkhuku, timaonetsetsa kuti incubator ikutentha madigiri 37.5. +Magetsi akazima zimakhala bwanji? Magetsi akazima mutha kulumikiza jeneleta koma ngati mulibe ndiye azime kwa masiku awiri mutafungatilitsa mazira amene adutsa masiku 18, ndiye mazira onse amaonongeka. Amenewo katayeni chifukwa anapiye amakhala afa. +Anapiye akabadwa, mumalowera nawo kuti? Amabwera mnyumba iyi. Ndi motentha chifukwa amakhala mwana wathu ali mchikuta. Kupanda kutentha kumeneku samachedwa kufa chifukwa ndi osakhwima. +Katemera mumawapatsa atakula bwanji? Tsiku lomwe abadwa timapereka katemera woteteza ku matenda. Kenaka timawapatsa madzi ndiye timadikira padutse mphindi 30 tisadawapatse zakudya. Zikatha sabata imodzi, timazipatsa katemera wa gumbolo, sabata yachiwiri timazipatsa katemera wa LaSota, sabata yachitatu timawapatsa gumbolo, yachinayi LaSota, ndipo yachisanu wa firepox. Sabata ya 6 timawagulitsa kwa alimi ndipo mlimi savutika nazo. Alimi amagula K500 mwanapiye mmodzi. +Nanga zakudya? Zakudya timapanga tokha, zikangobadwa kumene mpaka atakula timawapatsa chicken mash. +Katsoka: Mtsogoleri wa alakatuli Ulakatuli ndi limodzi mwa maluso omwe akuphukira kumene mdziko muno. Zaka zambiri zapitazo, anthu samatenga ndakatulo ngati njira yofalitsira uthenga kapena kuphunzitsa monga momwe zikukhalira pano. Pazaka zochepa zokha, alakatuli mdziko muno atumphuka ndipo anthu ambiri ayamba kukonda ndakatulo. Alakatuliwa adakhazikitsa bungwe lawo lomwe mtsogoleri wake ndi Felix Njonjonjo Katsoka. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere: Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Katsoka ndi mlakatuli wodziwa kuluka mawu Tandiuza dzina lako ndi komwe umachokera. +Ine ndine Felix Njonjonjo Katsoka. Ndimachokera mmudzi mwa Chingamba mboma la Ntcheu koma pano ndikukhala ku Nkhotakota. Ndidaphunzira za uphunzitsi koma ndimagwira ntchito ya zaumoyo kumbali ya zakudya zamagulu. +Utsogoleri wa alakatuli udaulowa liti? Ndidauyamba mchaka cha 2009. Malingana ndi malamulo athu, timayenera kukhala ndi zisankho zaka zisanu (5) zilizonse moti panopa tili kalikiriki kuthamangathamanga kuti tipeze ndalama zopangitsira nkhumano ina komwe tidzakhalenso ndi zisankho. +Kodi bungwe limeneli lidayamba liti? Bungweli lidayamba mchaka cha 1997 pomwe alakatuli adakumana kubwalo la masewero la Kamuzu Stadium. Ena mwa akatakwe omwe adali kumeneko ndi monga Laurent Namarakha, malemu Aubrey Nazombe, Edward Chitseko ndi malemu George Chiingeni. Pa 4 September, 1998, bungweli lidalembetsedwa kunthambi ya kalembera wa mabungwe. +Cholinga chake nchiya? Cholinga cha bungweli ndi kufuna kutukula luso la ulakatuli mMalawi muno komanso kufuna kufalitsa mauthenga ndi kuphunzitsa anthu kudzera mndakatulo monga momwe amachitira azisudzo kapena oyimba. +Kodi munthu amafunika chiyani kuti akhale mlakatuli? Choyambirira ndi kudzipereka kukhala ndi mtima ofunitsitsa kukhala mlakatuli. Sizilira kupita kusukulu, ayi, ndi luso ndithu lachibadwa. Ine sindidaphunzireko ndakatulo komanso alakatuli ambiri omwe ndimadziwa sadachite maphunziro a ndakatulo, ayi.katsoka Nanga ndakatulo yabwino imafunika kukhala ndi chiyani? Ndakatulo yabwino imayenera kukhala ndi phunziro, msangulutso komanso izigwirizana ndi zachikhalidwe kapena nkhani yomwe ikunenedwa. Mundakatulo muli ufulu wosankha mmene ukufunira kuti mavume azimvekera. Palibe malamulo akuti ndakatulo izimveka motere, ayi. Kwathu kuno, ndakatulo zambiri zimakhala zokhudza chikhalidwe cha Chimalawi, makamaka potengera chiphunzitso ndi malangizo. +Alimi konzekani kukolola madzi Mvula ya masiku ano ndi yanjomba. Zikatere mlimi amayenera kuchenjera kuti aphulepo kanthu ngakhale mvula itadula msanga. Ichi nchifukwa chake akatswiri pa zamalimidwe amalimbikitsa alimi kuti ayambe kukolola madzi a mvula. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Nthawi yokonzeka kukolola madziwatu ndi ino pamene mvula yayamba kale kugunda ndi madera ena mdziko muno ayamba kale kulandira mvula. +Mkonzi wa pulogalamu ya Ulimi Walero pawailesi ya MBC, Excello Zidana adati ngati alimi sachangamuka ndi ulimi wawo poyamba kukolola madzi, ndiye kuti ulimi uwavuta. +Madzi a mvula sayenera kumangotaika Mvula ya masiku ano mwaiona kale kuti ikugwa mwa njomba. Koma kwa alimi amene akukolola madzi, amathandizikabe chifukwa amagwiritsira ntchito madzi amene akolola pamene mvula yadula, adatero Zidana. +Pa momwe alimi angakololere madzi, Zidana adati pali njira zambiri zokololera madzi monga kupanga migula (akalozera) komanso kupanga mabokosi. +Ukapanga kalozera, mizere yonse yomwe ulime mmundamo imatsatana ndi kalozerayo, kusonyeza kuti mvula ikagwa madzi sathamanga. Komanso mukapanga mabokosi, madzi amaima ndi kudikha koma mukapanda kupanga izi, mvula ikagwa, madzi amathamanga kwambiri ndipo salowanso pansi, adatero Zidana. +Iye adati mgula kuti ulimbe uyenera kuti mlimi abzalemo udzu wa vetiva kuti madzi angachuluke bwanji sungagumuke. +Zidana adatinso kukumba dzenje kuti madzi azilowapo mvula ikamagwa ndi njira inanso yomwe alimi angakololele madzi. +Madzi amene asungidwa padzenjepo, mungathe kuwagwiritsira ntchito pamene mvula yadula. Komanso pakhomo panu muyenera kuika migolo yomwe mungasungire madzi. +Komanso kuthira manyowa ndi njira ina yokolorera madzi chifukwa chifukwa manyowa amasunga chinyezi chomwe chingakhale mmundamo kwa masiku pamene mvula yadula, adatero Zidana. +Anatchezera Kwawo sindidziwako Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Agogo, Ndinapeza mwamuna kudzera patsamba lino ndipo ndikuyamika chifukwa chondithandiza. Komano vuto langa ndi loti amakana kuti ndikadziwe kwawo, koma kwathu anapitako. Kumuuza kuti abwere ndi akwawo amati amakhala kutali. Ine ndimakhala ku Blantyre ndipo mwamunayo amakhala ku Lilongwe. Kodi ndiziti ndili pabanja? Ndine NF, Balaka Zikomo NF, Ndasangalala kuti munatha kupeza mwamuna kudzera patsamba lino. Zimatere bwenzi zikoma! Chomwe ndingakulangizeni nchakuti pamakhala dongosolo polowa mbanja. Kupeza mwamuna kapena mkazi ndi sitepe yoyamba imeneyo ndipo musanalowe mbanja pamafunika zinthu zingapo zichitike malingana ndi miyambo ndi chikhalidwe cha mtundu wanu. +Pakati pa Achewa ndi mitundu ina yambiri chigawo chapakati ndi ndi kummwera, ankhoswe a mbali zonse ziwiriakuchimuna ndi akuchikazi amayamba akumana kaye kuti adziwane kenaka amakonza chinkhoswe. Chinkhoswe chikatheka kwatsala ndi ukwati kapena mukhozanso kulowa mbanja malingana ndi mmene mwazikonzera. +Tsono ngati mwamuna wanuyu akukana kapena sakufuna kuti mukadziwe kwawo komanso akukana kubwera ndi akwawo, chilipo chimene akubisa. Munthu wotere nthawi zambiri amakhala kamberembere ndipo musamudalire kuti ali ndi chidwi ndi banja ameneyo. Munthu wachilungamo sasowa maonekedwe ndi machitidwe ake, koma uyu yekha ndikuona kuti ndi kapsala basi, musamale naye. Nkutheka kuti mwina ali kale ndi mkazi ameneyo ndipo akuopa kuti mukapita kwawo mukatulukira chinsinsi chake. +Mawu anga otsiriza ndikuti pokhapokhapo atalola kuti mukadziwe kwawo kapena abwere ndi akwawo kudzatomera ukwati, ndi bwino kusiyana naye ameneyo chifukwa adzangokutayitsani nthawi pachabe. +Samayankha foni Anatchereza, Ndili ndi chibwenzi ndipo tidagwirizana zomanga banja mtsogolomu. Iyeyu ndidakumana naye kumudzi kwathu komwe kuli makolo ake koma kwawo ndi ku Chitipa. Tsiku lina bwenzi langalo adanditsanzika kuti akupita kumudzi kwawo kuukwati wa mbale wake ndipo adandipempha kuti ndimugulire foni kuti tizilumikizana mosavuta poti yomwe adali nayo idali yovuta. Ine sindinavute, ndinamugulira foni yanyuwani. Kenako adandipempha ndalama yodyera komanso yoti agulire simukhadi ndipo nditamufunsa kuti akufuniranji simukhadi ina pomwe ina ilipo, adandiyankha kuti nambala yakale sakuifunanso. Sindinawiringule koma kumuchitira zomwe amafunazo chifukwa ndimamukonda. Koma chodabwitsa ndi choti atagula simukhadiyo sadandiuze nambala yatsopanoyo mpakana adanyamuka ulendo wakwawo. Padapita sabata ziwiri ndisakuidziwa nambala yanyuwaniyo ndipo kuti ndiziidziwa ndidachita kukafunsa kwa mayi ake. Kumuimbira sakuyankha ndipo ndikunena pano patha chaka tisakuyankhulana. Koma chodabwitsa nambala yanga adakagawa kwa azibale ake ku Chitipako ndiye ndiziti chiyani pamenepa, chikondi chidakalipo? Chonde ndithandizeni. +Tinkaimba limodzi kwaya Mdalitso suoneka pakudza munthu umangozindikira walandira mphatso koma osadziwa kuti yachoka kuti malingana ndi ntchito zomwe ukuchita monga momwe a mvula zakale adanenera kuti ntchito iliyonse ili ndi mphotho yake. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kudzipereka komwe adachita Joseph Kaluwa ndi Victoria Mdala Kaluwa mchaka cha 2014 posankha kutumikira Mulungu mnjira ya kwaya patchalitchi ya mpingo wa chikatolika wa Don Bosco ku Lilongwe kudawalunjikitsira kumoyo wina wopambana. +Awiriwa akuti amaimba kwaya limodzi ndipo kenako adagwa mchikondi atakhutitsidwa kuti iwo adalengedwa kuti adzakhale limodzi ngakhale kuti adabadwira ndi kukulira mbali ziwiri zosiyana za dziko lino la Malawi. +Joseph ndi Victoria tsiku la ukwati wawo Ndinkasangalala tikamaimba ndipo ndikamamva mawu ake a nthetemya. China chomwe chidanditenga mtima nchakuti amakonda kupemphera ndi kutumikira kutchalitchi, adatero Joseph. +Iye adati adayesetsa kuti awiriwa akhale pachinzake cha mchimwene ndi mlongo kwa miyezi yokwana 6 ndipo ataona kuti ena akhoza kungobwera nkuphumitsa adaganiza zomasuka ndipo mwa mphamvu ya Mulungu yomwe idawakumanitsa zinthu zidatheka. +Joseph adaonjeza kuti panthawiyo nkuti atangomaliza maphunziro ake a zowerengera ndalama koma asadayambe ntchito ndipo Victoria adali akadali pasukulu koma iwo sadawerenge izi pozindikira kuti Mulungu adzawatsogolera. +Tidalimba mtima ndipo tidasangalala kuti makolo ndi abale athu adatithandiza kwambiri mpaka tidapanga chinkhoswe ngakhale kuti chidali cha mnyumba koma pambuyo pake tidamanga ukwati woyera omwe tidakadalitsira ku Tchalitchi ya Don Bosco pa 29 September 2015, adatero Joseph. +Victoria adati sadalabadire zoti panthawiyo Joseph samagwira ntchito iliyonse chifukwa iyeyo adakonda munthu osati chuma ndipo adali wokondwa kwambiri makolo ake atavomereza chibwenzicho. +Iye adati ali ndi loto limodzi lokhala pa banja la ulemu ndi lowopa Mulungu monga momwe zilili pano.n Pemphero langa ndilakuti zipitirire monga momwe zilili pano. Ndili pabanja lokoma kwambiri ndipo ndimakonda mwamuna wanga kwambiri ndi ana anga atatu, adatero Victoria. +Joseph amachokera ku Nthalire mboma la Chitipa ndipo pano akugwira ntchito ku nthambi yolondoloza za momwe ndalama zikuyendera ya Financial Intelligence Unit ndipo Victoria amachokera kwa T/A Kwataine ku Ntcheu ndipo akugwira ntchito ku nthambi ya za nkhalango mboma. +Zungulizunguli mu Lilongwe Abale anzanga, inetu ukwati, nkhani ya ukwati, sindikamba nawo. Nkhani imeneyi, kwa ine ndimangoionera apo!!! Chifukwa chake nachi: Pali ana ena amene amaganiza kuti mayi awo ndi amami, chonsecho mayi awo ndi anti. Komanso pali ana ena amene amaganiza kuti bambo awo ndi adadi chonsecho ndi ankolo. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Musayerekeze kundifunsa kuti ndikutanthauza chiyani chifukwa sindikuyankhani. Ndakwiya nanu chifukwatu ndili muno mu Lilongwe momwe ndimakumana ndi anyamata ena. +Musayerekezenso kundifunsa ngati nkhani yake inali ya ukwati kapena ayi. Mukadziwa mukufuna mutani? Ndidatsika basi ya Lilongwe tsikulo chifukwa Abiti Patuma adandiuza kuti mzindawo uvuta. +Abale anzanga nanga nkadatani? Nkadachitanji chifukwatu ena adandiuza kuti uku nkwa gule ndipo ukwatiwo ndi wa abale. +Mwinatu sindidakuuzeni. Nthawi ija ankamanga ukwati anyamata aja, nthawi ya Moya Pete, ine ndidali pomwepo limodzi ndi Abiti Patuma. +Inde, anyamata aja adatchuka. +Chongoti mu Lilongwe fikeni, abale anzanga, inetu zikwama ndimachita kupanira ngati chiyani kaya! Tidayenda kamtunda ndithu ndipo tidaona umo apolisi amatapira ndalama muno mu Lilongwe: Kwa Biwi, inde Lower Biwi! Kugonetsa abambo olemekezeka pansi ati vakabo yawatapula! Umo mu Devils Street, ati kumene chiwanda cha Satana chidafikira, asungwana kukopa abambo; anyamata kufwamba abambo ndipo ana kutoleza zimene ataya abambo. +Lilongwe iyooo! Za kwinako sindikamba. Ati Kumpanda kwa Mafumu, inde ku Side kofikira Madonna; apa paakazembe ngakhalenso kumabedi ndiye eeeeh! Nkhani ili apa ndi ya anyamata amene tidawapeza akuchita zawo. Musadandaule, aka si koyamba, komanso kumbukirani anyamata a mu Mchesimu tsiku lina adafuna kuphwanya hotela ati chifukwa mwini hotela adazembetsa ana ena! Lilongwe iyooo! Tsono nkhani yakula apa ndi yakuti Moya Pete tsono wakumana ndi zija adakumana nazo Mfumu Mose nthawi ija ankafunsidwa ngati Mustafa angasiyire mngono wake Ajibu mpando woyanganira ife ojiya, osolola ndi osenza pano pa Wenela. +Makuponi otsiriza afika mzigawo Mabanja ovutikitsitsa tsopano akhoza kumwetulira kutsatira kaamba ka kubwera kwa makuponi otsiriza a zipangizo zaulimi zotsika mtengo. +Boma lati lalandira makuponi omaliza, zomwe zipangitse kuti alimi ovutikitsitsa 812 100 apeze zipangizozi mzigawo za pakati ndi kumpoto. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Makuponiwa abwera panthawi yomwe aphungu a ku Nyumba ya Malamulo komanso atsogoleri a mabungwe omwe si aboma akhala akudzudzula boma chifukwa cha kuchedwetsa pogawa makuponi komanso ganizo loyamba kugawa makuponi mchigawo cha kummwera. +Wachiwiri kwa mkulu woyendetsa ndondomeko ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo muunduna wa zamalimidwe, Osborne Tsoka, adatsimikiza za kufika kwa makuponiwa ndipo adaonjezera kuti boma lamaliza kusankha anthu omwe alandire makuponiwa mmaboma 27 ndipo boma la Dowa lokha ndiko ntchitoyi ikupitirira. +Tsoka adafotokoza: Tikudziwa kuti tikuthamangitsana ndi nthawi. Ichi ndi chifukwa chake tamwanza anthu kuti akhale akupereka makuponiwa kwa alimi mzigawo ziwiri zomwe zinali zisanalandire. Padakalipano, makuponi anyamulidwa kupita mmaboma omwe anthu adali asanalandire. +Tikakamba za maboma, boma la Dowa ndilo latsala kuti timalize ntchito yosankha anthu omwe alandire makuponiwa. Ndikukhulupirira kuti pofika kumapeto a sabatayi ntchitoyi ikhala itatha. +Poyankhula mwapadera, nduna ya zaulimi ndi chitukuko cha madzi Dr Allan Chiyembekeza adati sadatekeseke ndi chikayiko cha mabungwe omwe si aboma chakuti ndondomekoyi chaka chino ikumana ndi zokhoma. +Sabata yatha, boma lidalandira makuponi oyamba ofikira anthu 687 900 mchigawo cha kumwera. +Koma potsirapo ndemanga pa anthu ovitikitsitsa omwe alandire makuponiwa chaka chino, mafumu ena, maka mchigawo cha kumpoto adandaula kuti kusankha maina sikunayende bwino chaka chino chifukwa ena omwe asankhidwa kuti alandire nawo si anthu ovutikitsitsa, koma opeza bwino chifukwa ali mzintchito zolipidwa pamwezi. +Ku Rumphi, nyakwawa ina ya mdera la Gulupu Chikulamasinda kwa Themba la Mathemba (Paramount Chief) Chikulamayembe, idati ndi yokhumudwa chifukwa mwa anthu 9 omwe alandire makuponiwa mmudzi mwake asanu ndi oti sali pamudzipo koma mzintchito monga ku Blantyre, ku Lilongwe ndi ku Mzuzu komanso wina ndi mphunzitsi ku Kasungu. +Inde ndi a mmudzi mwanga, koma si ovutikitsita. Ine mwini wakene ndimagwira ntchito ku Blantyre koma dzina langa latuluka pamndandanda wa omwe apindule ndi makuponiwa kusiya anthu ovutikitsitsa mmudzi mwanga. +Sindidziwa kuti amasankha bwanji mainawa chifukwa akadatifunsa mafumufe kuti woyenera ndani kulandira makuponi tikadawapatsa maina a anthuwo, osati kusankha okha. Okhala ndi anthu ndan, iwowo kapena ife mafumu? idafunsa mfumuyo, yomwe sidafune kuti itchulidwe poopera mawa. +Boma lapempha amalawi adekhe pa za mathanyula Boma lapempha aMalawi kuti adekhe pankhani yoimitsa lamulo loletsa umathanyula mdziko muno. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Polankhulapo mkati mwa sabatayi, mneneri wa boma Jappie Mhango adati kuthamanga si kufika ndipo nkhaniyo ifunika iunikidwe bwino ndi akatswiri a za malamulo. +Mhango adati masiku akubwerawa Amalawi apereka maganizo awo pankhani ya mathanyulayi ponena kuti atolankhani ndiwo akukokomeza polemba ndi kuulutsa zambiri zokhudza nkhanizi. +Mneneriyu adauza Tamvani kuti boma lapanga chiganizo chopereka nkhaniyo kwa akatswiriwo kuti akamaliza kuunika alengeze zomwe Amalawi akuyenera kuchita pankhaniyi. +Adachititsapo chinkhoswe: Chimbalanga (kumanja) ndi Monjeza Tikufuna kutsatira ndondomeko zoyenera, tisathamange ayi, Mhango adatero, nkuonjezera kuti akatswiri a zamalamulowo ndiwo alangize boma pa ndondomeko yoyenerayo. +Mundimvetsetse, sindikuti tikhala ndi riferendamu, ayi, koma ndikuti atilangiza pa za ndondomeko zoyenera kutsatidwa kuti Amalawi apereke maganizo awo pankhaniyo, adatero Mhango. +Koma padakalipano zipani zotsutsa boma komanso mafumu adzudzula boma poimitsa lamulo lomanga amathanyula lisanamve maganizo a anthu a mdziko muno. +Polankhulapo msabatayi, wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Peoples Party Kamlepo Kalua adati izi zikukhala ngati kutengera Amalawi konyongedwa. +Kalua adati umathanyula ndi khalidwe losemphana ndi zomwe chikhulupiriro ndi chikhalidwe chawo chimanena. +Kodi mukundiuza kuti tivomereze umathanyula ndi kusiya chikhulupiriro chathu chifukwa cha thandizo lochokera kunja? Apatu tikupita kokanyongedwa ndithu, adatero Kalua. +Iye adati Amalawi aone zakutsogolo osati zalero chifukwa umathanyula udzapha tsogolo la dziko lino. +Ndalamazo mudya lero, ndipo musangalala, koma ganizani za tsogolo lanu, Kalua adatero. +Koma Inkosi ya Makhosi Mmbelwa adati ngakhale mafumu sadakhale pansi kukambirana za nkhaniyi chifukwa chosowa thandizo, sakuvomereza zoimitsa lamulo loletsa umathanyula mdziko muno. +Mmbelwa adati umathanyula ukusemphana ndi chikhalidwe cha Amalawi ndipo si zololedwa. +Masiku akubwerawa tikumana ngati mafumu kuti nafe tilankhulepo pankhaniyi, yomwe yautsa mapiri pachigwa, Mmbelwa adatero. +Sabata yatha mneneri wa chipani cha PP Ken Msonda, polankhula mwa yekha adati Amalawi ayenera kupha ochita mathanyula. Bungwe la maloya mdziko muno la Malawi Law Society (MLS) lidati apa Msonda adalakwa ndipo lidati Msonda ayenera kumangidwa. +Bwalo la milandu la majisitileti ku Blantyre laitanitsa Msonda kuti akaonekere kubwalolo pa 22 January. +Koma polalikira kumpingo wa South Lunzu CCAP ku Machinjiri mumzinda wa Blantyre, Msonda adati sasintha mawu ake. Iyi si nkhondo ya Msonda koma nkhondo ya ana a Mulungu kulimbana ndi mdyerekezi, adatero iye mu ulaliki wake. +Izi zili choncho, mmodzi mwa omenyera ufulu wa anthu Gift Trapence adati ochita mathanyula ali ndi ufulu wachibadwidwe ndipo Amalawi sayenera kupondereza anthuwa. +Malamulo oyendetsera dziko lino komanso malamulo a dziko lapansi amaneneratu kuti si bwino kuphwanya ufulu wa ena, adatero Trapence. +Nkhani ya mathanyula yayala nthenje kuchokera pamene anyamata awiri Kelvin Gomani ndi Cuthbert Kulemeka adagwidwa ndi apolisi powaganizira kuti amachita za u ndevu ku ndevu. +Maiko ndi mabungwe othandiza dziko lino adati aleka kupereka thandizo kudziko lino ngati awiriwo satulutsidwa. Boma lidatulutsa awiriwo. +Tinkakalongosola za ntchito Okaona nyanja amakawonadi ndi mvuu zomwe. Mawuwa apherezedwa ndi ukwati wa Amos Mazinga wa ku Dowa mmudzi mwa Ngozi T/A Chiwere ndi Regina Mkonda wa ku Mulanje mmudzi mwa Reuben. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Awiriwa akuti adakumana kuofesi ya maphunziro ku Nathenje mu 2014 atamaliza maphunziro a zauphunzitsi komwe amakolongosola za komwe azikagwirira ntchito. +Amos adati iye atangomuona Regina, mtima wake udadumpha kwambiri. +Amos ndi Rehina kupsopsonana tsiku la ukwati wawo Ndine mmodzi mwa anthu omasuka ngakhale pagulu koma tsikulo ndidaona nyenyezi yothobwa mmaso, adatero Amos. +Iye akuti panthawi yomwe iwo amayembekezera kuthandizidwa, mpamene adapeza mwayi wolankhulana ndi msungwanayo ndipo adacheza bwino mpaka kupatsana nambala za foni. +Kusiyana kwa pamenepo kudali madzulo atalandira thandizo koma kudali kusiyana pamaso chabe chifukwa macheza awo adapitirira kudzera palamya. +Tidakhala nthawi yaitali tikuchezerana palamya mpaka tsiku lina nditalimba mtima ndidayambitsa nkhani ya chikondi koma kunena zoona ndidalimbana naye mpaka adatheka, adatero Amos. +Iye akuti chikondi chake pa Regina chidakula kwambiri kaamba ka khalidwe lake lokonda kupemphera, kuchita zinthu mwa nzeru ndi modzilemekeza komanso mwasangala. +Regina adati iye poyamba adamutenga Amos ngati mchimwene koma pangonopangono chikondi chidayamba kumugwira moti samafunanso kuti Amos adzagwe mmanja mwa munthu wina koma iye. +Iye adati ngakhale amakanakana poyamba, mtima wake udali utalola kale koma amafuna kuona ngati Amos adalidi munthu wachilungamo wosangofuna kumuseweretsa. +Sindidafune munthu woti kugwa naye mchikondi panthawi yochepa kenako nkukhumudwitsidwa ndiye ndimayenera kuonetsetsa kuti ndikudzipereka mmanja oyeneradi, adatero Regina. +Ukwati adamangitsa kumpingo wa CCAP. +Sabuside yayamba ndi njengunje Pulogalamu ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo ya sabuside ya chaka chino yayamba koma zokhoma zilipo zambiri kuyerekeza ndi zaka zammbuyomu, nduna ya zamalimidwe Allan Chiyembekeza yavomereza. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Polankhula ndi Uchikumbe, Chiyembekeza adati pulogalamuyi yayamba ndi jenkha chonchi kaamba ka mavuto ena monga a zachuma chifukwa boma tsopano likudzidalira palokha pachuma chake. +Ndunayo idati ngakhale ntchitoyi yayamba ndi mavuto oterewa, Amalawi asataye mtima chifukwa boma kudzera muundunawo likudzipereka kuti alimi asavutike. +Anthu kudikira kugula zipangizo zotsika mtengo chaka chatha Tikuvomereza kuti zinthu sizidayambe bwino koma sizikutanthauza kuti zinthu zaipiratu ayi chifukwa padakalipano zipangizo zayamba kale kupita mmadera moti alimi asataye mtima zinthu ziyenda, adatero Chiyembekeza. +Ndunayo idati polingalira mavuto a mayendedwe nthawi ya mvula, ntchitoyi yayamba mmadera ovuta kufikira mdziko lose la Malawi polingalira kuti mvula ikayamba mmadera oterewa galimoto zonyamula zipangizozi zimatitimira kapena kugwa mmatope. +Tayambapo makamaka mmadera ovuta kufikira mvula ikagwa. Panopa madera ambiri oterewa alandira kale zipangizo moti alimi akungodikira makuponi ogulira kuti akagule, adatero Chiyembekeza. +Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a zaulimi wa Civil Society Agriculture Network (Cisanet) Tamani Nkhono Mvula adati boma lachita bwino kubwera poyera nkunena momwe pologalamuyi ikuyendera kuti alimi azidziwiratu zochitika. +Nkhono adati kawirikawiri zinthu zimaonongeka chifukwa chobisa momwe zinthu zilili zomwe zimachititsa kuti alimi azidzidzimutsidwa nthawi yothaitha zinthu zitasokonekera kale. +Pamenepa ife tiyamikire boma chifukwa lapanga zazikulu kubwera poyera. Nthawi zambiri chilungamo ngati ichi chimabisidwa chifukwa cha ndale koma mapeto ake zinthu zimasokonekera,adatero Nkhono. +Iye adati alimi panopa akhale kalikiliki mminda kuyembekeza mvula yobzalira osatengera kuti boma lalankhula bwanji chifukwa iwowo ndiwo amalima osati boma lomwe limangothandizapo. +Alimi ambiri pano ali mminda kukonza kapansi kuti mvula ikangogwa abzale mbewu koma akuti ali ndi nkhawa chifukwa sakudziwa kuti mbewu ndi zipangizo zina ngati feteleza azipeza liti poti sadalandilebe makuponi ogulira. +Amos Dziyende ndi mmodzi mwa alimi omwe adakonza kale munda wake ndipo adati nkhawa yake ili pawiri: Mtengo wa zipangizo ndi nyengo yogulira poti mpaka lero sadalandirebe makuponi ogulira. +Tidakonzeka koma tikumva kuti mtengo wa zipangizo chaka chino wakwera ndiye kaya zitha bwanji komanso mpaka pano makuponi sitidalandire, adatero Dziyende. +Panopa mvula yagunda kale mmadera ena ndipo nthawi iliyonse madzi akhala akugwa pansi kuti dzinja. +Msika wa zondeni ngosayamba Katswiri wa zamadyedwe mdziko muno, Chrispine Jedegwa, akupanga ndi kugulitsa ufa wa mbatata ya kholowa yamakolo yotchedwa zondeni yomwe akuti ili ndi ufa wapamwamba wopatsa thanzi. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Anthu ambiri adazolowera kuti ufa umapangidwa kuchokera kuchimanga ndi chinangwa basi koma katswiriyu wati phindu lochokera mmbatata limachuluka mbatatayo ikagayidwa nkugulitsa ufa wake. +Alimi ambiri sakonda kulima mbatata ya zondeni chifukwa sibereka kwambiri koma chomwe sadziwa nchakuti mbatatayi ili ndi mphamvu ya mankhwala ndipo muli ndalama zochuluka, adatero Jedegwa. +Jedegwa: Ufa wa zondeni tikaukonza umakhala ngati uwu Iye adati mbatatayi ikacha ndipo mukaimuka bwinobwino mukaigaya mukhoza kupanga ufa wophikira phala kapena chakudya china chilichonse ndipo munthu akadya phalalo thupi lake limakulupala. +Mkuluyu adati alimi alime mbatata ya mtunduwu kwambiri powatsimikizira kuti msika wake ulipo wosayamba. +Pakalipano mbatatayi ikulimidwa kwambiri ndi alimi a ku Thyolo, Phalombe, Kasungu ndi Mchnji koma sakukwanitsa pomwe ife timafuna moti alimi omwe akufuna kupha makwacha alime mbatata yamtunduwu ndipo tikulonjeza kuti tidzawagula, adatero Jedegwa. +Iye adatinso alimi atafuna mbewu ya mbatatayi yobereka kwambiri akhoza kukumana ndi akuluakulu a kampani ya C & NF omwe akupanga ufawu chifukwa mbewuyi alinayo yambiri. +Alimi ambiri amadandaula kuti amalephera kulima mbewu zina polingalira nkhani ya msika koma Jedegwa watsimikiza kuti kampani yawo njokonzeka kugula mbatata yonse ya zondeni yomwe alimi angalime. +Jedegwa adati kupatula kuti ndi chakudya, ufa wa mbatata ya zondeni ndi mankhwala othandiza kumatenda osiyanasiyana monga mtima, kuthamanga kwa magazi, shuga, zilonda zammimba ndi kuphwanya kwa minofu. +Mafumu okwatitsa ana athothedwa Kachindamoto achotsa mafumu anayi Ana 549 abwerera kusukulu ku Dedza Kampeni yothamangitsa ana kubanja kuti abwerere kusukulu yafika pagwiritse mboma la Dedza pamene T/A Kachindamoto wathotha mafumu anayi pokolezera maukwatiwa. +Kachindamoto: Tidagwirizana malamulowa Ngakhale gawo 11 (1) la malamulo okhudza mafumu la mchaka cha 2000 limati pulezidenti wa dziko yekha ndiye ali ndi mphamvu yochotsa mfumu, Kachindamoto wati palibe cholakwika iye kuthotha mafumuwo. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Iye wati mphamvuzo akuzitenga mmalamulo amene mdera lake adakhazikitsa chaka chatha wolanga mfumu yovomereza maukwati wa ana. Tidakhazikitsa malamulo athu amene tidavomerezana ndi anthu komanso mafumu tonse kuno kuti ngati papezeka mfumu yopsepserezera ukwati wa ana, imeneyo iyenera kuchotsedwa. +Ichi nchifukwa chake mafumuwa atapezeka olakwa, ndidawaitana anthu onse ali pamenepo pamene ndidalengeza kuti ufumu wawo watha. Iwo achotsedwa chifukwa choswa malamulo, adatero Kachindamoto. +Koma mneneri wa maboma angono Muhlabase Mughogho wati ngakhale pulezidenti ndiye ali ndi mphamvu yochotsa mfumu, malamulo amene Kachindamoto ndi anthu ake adakhazikitsa alinso ndi mphamvu yothotha mfumu ngati yalakwitsa. +Nkhani imeneyo ife sikutikhudza, imeneyi ndi yawo. Ngati adagwirizana kuti mfumu izichotsedwa ikasemphana ndi malamulo amene adagwirizana, ndiye palibe nkhani pamenepa, amenewo ayenera kumvera zomwe adagwirizana, adatero Mughogho. +Kachindamoto akuti kupatula anthu ndi mafumu amdera lake amene adagwirizana ndi malamulowa, nawo amabungwe omenyera kuti ana apite kusukulu akusangalala ndi ndondomekoyi. +Iye wati, adasankha kuti mfumu izilandira chilango chifukwa ukwati kapena chinkhoswe si zimachitika mdera popanda mfumu kudziwa. +Kukakhala ukwati kapena chinamwali, banja lomwe likupangitsalo, limakadziwitsa mfumu pamene amakapereka nkhuku. Apa ndiye kuti anthuwa ali ndi chilolezo chochititsa ukwatiwo. +Podziwa izi, nchifukwa tidati mfumu yomwe ilandire nkhukuyo kapena yomwe ivomereze ukwatiwo idzalangidwa poichotsa pampando, adatero Kachindamoto. +Chifukwa cha malamulowa, Kachindamoto wati ana 549, amuna ndi akazi omwe abwerera kusukulu pamene asiira ana awo kwa makolo. +Iye adati mafumu amene achotsedwawa akhala akuvomereza ukwati wa ana polandira nkhuku kwa eti ukwati zomwe ndi zosemphana ndi malamulo awo. +Mafumuwa akhala akulandira nkhuku ngakhale amadziwa kuti amene akuchititsa ukwatiyo ndi mwana woyenera apite kusukulu. Mafumu atatu ndidawachotsa chaka chatha pamene inayo ndidaichotsa chaka chomwe chino, adatero Kachindamoto yemwe ali ndi magulupu 51. +Nyakwawa Galuanenenji yomwe ufumu wake udatha povomereza ukwati wa mtsikana wa zaka 15, yati idadandaula kuti ufumu wake watha komabe sadaone cholakwika. +Malamulo tidavomereza tokha, komabe pena zidavuta pamene ndidavomereza ukwati wa mtsikana wa zaka 15. Adandiitana pagulu ndipo gogochalo adalengeza kuti ufumu wanga watha. Mutu udakula, ndipo mmimba mudatentha kuti ufumu wanga watha, adatero Galuanenenji. +Panopa ndidakapepesa kwa gogochalo ndipo ndidakathetsanso banjalo, panopa mwanayo wabwerera kusukulu. Chifukwa choti ndidapepesa komanso kuti ukwatiwo ndidakathetsa, amfumuwa andibwezeretsa pampando, idatero nyakwawayi. +Mmodzi mwa atsikana amene abwerera kusukulu, Judith Kabango wati ndiwokondwa ndi malamulo amene mudzi wawo udagwirizana. +Ndidatengana ndi mwana mnzanga wapasukulu. Panthawiyo nkuti ndili sitandede 7, pano ndili 8 ndipo mayeso apitawa ndidakhala nambala 4. Ndikufuna ndiphunzire ndipo ndikufunitsitsa ndidzagwire ntchito ya utolankhani, adatero mtsikanayu yemwe mwana wake ali ndi zaka 4. +Bambo ake a Judith, Stanstance Kabango ammudzi mwa Kalonga ati ndiwokondwa kuti mwana wawo tsopano wabwerera kusukulu. +Iwo ati adali wokhumudwa kuti mwana wawo yemwe adamukhulupirira kuti adzapita patali ndi sukulu wakalowa banja. +Ankadziwana ndi mayi anga Kale makolo amachita kusankhira ana awo munthu wokwatirana naye, koma pano zinthu zidasintha ngakhale kuti makolowo akhoza kungokhala muni wowalitsa kuti ana aonane nkukondana. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Anthu ambiri apezapo mabanja chifukwa chakuti makolo awo kapena abale awo ena amachezera limodzi ndipo kudzera mukucheza kwawoko ana awo adaonana ndi kukondana mpaka lero ndi banja. +Lucky ndi Sheira patsiku la chinkhowe Njira ngati iyi ndimo lidayambira banja la Lucky Madaika wochokera kwa Chipyali mboma la Balaka ndi Sheira Kachitseko wa kwa Bubua, T/A Makwangwala ku Ntcheu. +Awiriwa kuti akumane nchifukwa chakuti Lucky ankapitapita kunyumba kwa Shiera malingana ndi bizinesi yake ya zamakompyuta kukaonana ndi mayi a Sheira ngati kasitomala wake. +Ukutu akuti kudali kumayambiriro a chaka cha 2015 ndipo atapita kangapo kunyumbako, adalephera kuugwira mtima mpaka adapempha nambala ya lamya kuti aziimbirana nkumacheza koma kenako chibwenzi chidayambika. +Tidakhala pachibwenzi kwa miyezi ingapo kenako tidaganiza zopanga chinkhoswe ndipo zonse zoyenera monga kukaonekera kumakolo ndi zina zitachitika, chinkhoswecho chidachitikadi ku Area 47 mumzinda wa Lilongwe, adatero Sheira. +Iye adati mmiyezi 7 ikudzayi awiriwa adzakhala akuvekana mphete, makamaka pa 9 July, 2016 mumzinda womwewu wa Lilongwe. +Lucky adati aiwiriwa amakhulupirira kuti powalenga, Mulungu adakonza kuti adzakhala limodzi poona chikondi chomwe amapatsana komanso akuti pali zambiri zomwe onse amakonda kapena kudana nazo. +Agumula chiliza nkutengamo alubino Adaikidwa mmanda pa 27 May mchaka cha 2000. Koma zodabwitsa zachitika pa 17 October 2015 pamene anthu olusa agumula chiliza ndi kuthawa ndi mafupa. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Izi ndizo zachitika mmanda ena kwa Mkanda, T/A Kalolo mboma la Lilongwe komwe anthu ena afukula maliro a alubino amene adaikidwa mmanda zaka 15 zapitazo. +Malinga ndi T/A Kalolo, mandawo adagonekapo John Mphoka yemwe adabadwa mu 1952 ndipo adamwalira pa 25 May 2000 ndi kuikidwa pa 27. +Malinga ndi Kalolo, malemuwo adali amtundu wa chi alubino, zomwe zikupereka maganizo kwa mfumuyi kuti alipo mdera lawo amene akukhudzidwa ndi nkhaniyi. +Nanga inu munthu tidamuika zaka 15 zapitazo, ndiye ngati ndi alendo iwowo adziwa bwanji kuti pamenepa tidakwirirapo munthu wa chi alubino? Alipo konkuno amene akukhudzidwa ndi izi komabe tikufufuza, Kalolo adatero Lachitatu. +Kalolo adati adazindikira kuti malemuwo abedwa Lolemba pamene mmudzimo mudagwa thambo lakuda. Iye adati pamene adzukulu amati akakumbe nyumba yoti malemuwo akagone, ndi pamene adaona malodzawo. +Pamene timafuna kukumbapo padayandikana ndi pomwe tidagoneka malemuwo. Ndiye mwambo wokumba udasokonekera kaye pamene tidathamangira kukadziwitsa apolisi, adatero. +Pamalopo akuti padangotsala bulangete lokha koma bokosi lidali litawola kale. Apolisi atadzafukula akuti adapeza mafupa 22 angonoangono koma mafupa ena onse adatengedwa ndi achiwembuwo. +Mneneri wapolisi mumzinda wa Lilongwe Kingsley Dandaula adati nkhaniyo ndi yoona koma akuyenera alandire lipoti kuchokera kwa apolisi awo kuderalo. +Tamvadi za nkhaniyi koma tikudikirabe apolisi kuderalo kuti atipatse zomwe apeza komanso kuti tidziwe momwe nkhaniyi ikuyendera, adatero Dandaula. +Tili pa nkhani yonga iyi, chisoni chidagwira anthu ammudzi mwa Nyundo kwa T/A Mwansambo mboma la Nkhotakota pamene anthu ena adafukula mafupa pamene amalima mmunda. +Malinga ndi mneneri wapolisi ya Nkhotakota, Williams Kaponda, izi zidachitika mu esiteti ya Basal pamene anthu amalima mmundamo pa 18 October. +Anthuwo adali akugwira ntchito yolima mmundamo, koma adadzidzimuka pamene adatema fupa. Podabwa, iwo adakauza bwana wawo amene adadzatidziwitsa, adatero Kaponda. +Kaponda adati pamodzi ndi achipatala, adathamangira kumundako komwe adakapeza mafupawo ndipo zidatsimikizika kuti adali amunthu amene akumuganizira kuti adamwalira mchaka cha pakati pa 2013 ndi 2014. +Koma mayi wina komweko akuti wazindikira zovala za malemuwo kuti adali amuna ake amene adasowa. +Osabweza ngongole ya Mardef ali mmadzi Anthu amene sadabweze ngongole ya Malawi Enterprise Development Fund (Mardef) ali mmadzi pamene ayamba kuona zakuda. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ngongole ya Mardef idayamba nthawi ya ulamuliro wa Bingu wa Mutharika pomwe amapereka ndalama kwa achinyamata kuti ayambire bizinesi. Koma ambiri mwa anthuwo sanabweze ngongoleyo. +Malinga ndi anthu ena amene tacheza nawo mboma la Kasungu, anthu amene sadabweze ngongoleyi ayamba kumangidwa pamene ena akuwalanda katundu. +Mneneri wa Mardef Isaac Mbekeani watsimikiza kuti bungwe lawo layamba kutoleradi ngongoleyo mboma la Kasungu ndi maboma ena. Koma iye adati timupatse mpata kuti afufuze kuchuluka kwa anthu amene akuwafufuza ngakhalenso ndalama zimene zikufu nika. +Tumizireni mafunso ndipo ndikuyankhani tsatanetsatane wake za nkhaniyi, adatero Mbekeani Lachinayi koma pofika Lachisanu nkuti asadayankhe mafunsowo. +Koma nyakwawa Alamu ya pamsika wa Nkhamenya adatsimikizira Msangulutso kuti anthu ena anjatidwa koma sadapereke zambiri pankhaniyi. +Mmudzi mwanga mulibe amene ali ndi ngongoleyi chifukwa iwo amene adakongola nawo adabweza kale ngongoleyo, koma madera ena mboma lino ndiye anthu ali pakalapakala, idatero mfumuyo. +Mayi ena amene sadafune kutchulidwa koma akukhala pamsika wa Nkhamenya mbomalo, adati anthu amene sadabweze ngongoleyi ayamba kubisala. +Pamene zidamveka mwezi watha kuti amene sadabweze ngongoleyi ayamba kuwamangitsa, anthu ena asamuka kuno pamene ena akumabwera usiku wokhawokha ndi ena athawiratu. +Ngati sudabweze ngongoleyi akumakumangitsa, apo ayi ena akumawatengera zinthu monga mwa mgwirizano wa ngongoleyo, adatero. amene adakongola nawo adabweza kale ngongoleyo, koma madera ena mboma lino ndiye anthu ali pakalapakala, idatero mfumuyo. +Mayi ena amene sadafune kutchulidwa koma akukhala pamsika wa Nkhamenya mbomalo, adati anthu amene sadabweze ngongoleyi ayamba kubisala. +Pamene zidamveka mwezi watha kuti amene sadabweze ngongoleyi ayamba kuwamangitsa, anthu ena asamuka kuno pamene ena akumabwera usiku wokhawokha ndi ena athawiratu. +Gulani mbewu kwa ogulitsa ovomerezekaUnduna Unduna wa malimidwe walangiza alimi kuti ayenera kugula mbewu kuchokera kwa ogulitsa ovomerezeka okha poopa kugulitsidwa mbewu zoonongeka. +Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Mlembi wamkulu muundunawu, Erica Maganga, wati alimi aike patsogolo mbewu zopezeka msitolo komanso mabungwe amene adalembetsa ku undunawu. +Alimi ayenera kugula mbewu malo ovomerezeka okha Kugulitsa mbewu popanda chilolezo chochoka ku undunawu ndi mlandu waukulu. +Mbewu iyenera kugulitsidwa ndi okhawo ali pa mgwirizano ndi kampani zopanga mbewu. +Ogulitsa mbewu otere amaphunzitsidwa bwino za kagulitsidwe ka mbewuzo komanso kasungidwe kake, adatero Maganga. +Malinga ndi maganga, ogulitsa mbewu ovomerezeka amalandira chiphaso chogulitsira mbewu chomwe chimagwira ntchito kwa chaka chimodzi. +Iye adati onse ofuna kugulitsa mbewu ayenera kulembera kalata ku nthambi yoona za mbewu muundunawu ya Seed Certification and Control Unit. +Ogulitsa amene sakwaniritsa ndondomeko zomwe amapatsidwa pogulitsa mbewu amalandidwa chiphasocho. Cholinga chachikulu nchakuti alimi azigula mbewu zovomerezeka komanso zomwe sizidaonongeke, adatero Maganga. +Maphunziro a chidyerano cha chimbudzi athandiza Moyo wasintha ndipo kamphepo kayaziyazi kakudutsa tsopano mmidzi 13 yozungulira dera la T/A Njewa ku Lilongwe anthu atasintha khalidwe lochitira chimbudzi paliponse nkuyamba kugwiritsa ntchito zimbudzi. +Zaka 51 chilandirireni ufulu odzilamulira, anthu kuderali amadalirabe tchire ndi kuseli kwa mitengo akafuna kudzithandiza kufikira pomwe bungwe la Plan International lidawafikira ndi maphunziro akuipa kochitira chimbudzi paliponse. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Bungweli lidaphunzitsa anthuwa kuti akamachitira chimbudzi paliponse ndiye kuti akuchita chidyerano cha zopambukazo pakati pa wina ndi mnzake zomwe zingawabweretsere matenda otsegula mmimba ndi mmapapo kaamba kafungo loipa. +Njewa adatsimikiza kuti kwanthawi yaitali anthu mdera lake samadziwa kufunika kwa chimbudzi ndipo mmimba mukafunda amangolowa patchire nkukadzithandiza ndipo adati pachifukwachi, mderali mumabuka matenda osiyanasiyana pafupipafupi. +Padalibe zoti wamkulu kapena mwana ayi. Aliyense amati akamva mmimba, kokapumira kudali kutchire ndiye padalibe zaulemu chifukwa nthawi zina mwana amatha kupezerera wamkulu akudzipeputsa komanso matenda samati abwera liti, adatero Njewa. +Iye adati nthawi zina alendo amadziwira fungo kuti afika mdera la Njewa chifukwa chimbudzi chidali ponseponse mpaka liti, adatero Njewa. +Iye adati nthawi zina alendo amadziwira fungo kuti afika mdera la Njewa chifukwa chimbudzi chidali ponseponse mpaka anthu kumachita nkhawa poyenda mtchire kuopa kuponda chimbudzi cha munthu wina. choyamba adafotokozera anthuwo kuti amadyerana chimbudzi pazomwe amachitazo. +Mlongoti adafotokoza kuti zidawatengera miyezi iwiri kuti anthu amvetsetse momwe amadyera chimbudzi cha anzawocho ndipo atamvetsetsa adayamba kukumba zimbudzi zomwe akugwiritsa ntchito pano. +Lidali dera lomvetsa chisoni kwambiri pankhani yaukhondo. Poona kuti tivutika kumvana nawo msanga, tidagwiritsa ntchito chionetsero. +Apatsidwa upangiri wa chitukuko Anthu okhala kumudzi ali ndi mphamvu komanso ufulu woitanitsa chitukuko cha mtundu wina uliwonse kudera lawo kotero kuti kudzipereka pantchitoyo ndi komwe kumafunika. +Mkulu wa bungwe la National Initiative for Civic Education (Nice) mboma la Mulanje a Twambilire Mwalubunju ndiye adanena izi Lachisanu sabata yapitayo pamene bungwe lawo lidakayendera anthu aku dera la mfumu Chonde mbomalo. +Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Malingana ndi anthu omwe adasonkhana pa mkumanowo, kuphatikizapo mfumu Chonde, ntchito zachitukuko kuderalo sizimayenda bwino kwenikweni chifukwa anthu a kumudzi sadziwa ufulu komanso mphamvu zawo pa chitukuko. +Ena mwa omwe adafika kumsonkhanowo Chitukuko chimayenda pangonopangono nthawi zambiri chifukwa anthu ambiri akumudzife sitidziwa udindo, ufulu komaso mphamvu zathu pa chitukuko. Timangoona ngati kubweretsa chitukuko kudera ndi udindo wa boma, mabungwe ndi ena otero. Mwachitsanzo anthu salankhulapo akamakumana ndi mavuto osiyanasiyana monga kusowa kwa zipangizo za ulimi kapena za umoyo mzipatala, adatero Chonde. +Mfumuyo idaonjezera kuti nthawi zambiri ntchito za chitukuko kudera lakelo siziyenda bwino chifukwa palibe mgwirizano weniweni pakati pa anthu a kumudzi, andale komanso a mabungwe ena. +Zimakhala zomvetsa chisoni kuona kuti anthu ena amangobwera mmudzi kudzayamba ntchito zachitukuko popanda dongosolo lenileni. Ukafunsa amakuyankha kuti adzera ku maofesi aboma. Zotsatira zake chitukuko chikamapanda kuyenda, ndi anthu akuderako omwe amavutika osati anthu andale kapena mabungwe, idatero nyakwawayo. +Koma mmalo mwake, bungwe la Nice lidapereka upangiri watsopano kwa anthu akwa Chonde wa momwe angathandizire kuunika komanso kutengapo gawo pantchito za chitukuko mdera lawo. +Kuyambira lero, munthu, bungwe kapena wa ndale asadzabwere kuno kudzakunamizani kuti ndi katswiri wa chitukuko chifukwa katswiri wamkulu ndinu. Popanda inu kutengapo gawo kapena kufunsa ndondomeka zachitukuko kudera kwanu ngati zinthu sizikuyenda, ndiye kuti mudzaononga zinthu nokha. Inuyo ndiye ani ake chitukuko amene mukuyenera kuonetstats kuti zinthu zikuyenda, adatero Mwalubunju. +Bungwe lilangiza alimi kubzala mbewu zopirira Malingana ndi kabweredwe ka mvula ya masiku ano, akatswiri alimbikitsa kuti alimi asamangoganiza za mbewu zamakono koma mbewuzo zizikhala zopirira kuchilala zomwe akuti zili ngati inshuransi kwa mlimi. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Lanena izi ndi bungwe lolimbikitsa kutukula ulimi wa trigu ndi chimanga ku mmawa ndi kummwera kwa Afrika la International Maize and Heat Improvement Centre (CIMMYT) lomwe lakhazikitsa polojekiti ya zaka 4 yotukula mbewu zopirira kukagwa ngamba. +Mkulu wa bungweli Dr Kennedy Lweya, adati mbewu zamakono zopirira ku ngamba zili ndi ubwino waukulu kuposa mbewu zamakono chabe zomwe alimi ambiri amalima chifukwa ngamba ikagwa zimaonongeka. +Mlimi kusamalira mmera mmunda wachimanga: Nkofunika kusankha mbewu yopirira kuchilala kuti zokolola zichuluke Zokolola zimachuluka ndi 40 pa 100 iliyonse mlimi akabzala mbewu zamakono zopirira ngamba. Mwachitsanzo, kubzala mbewu yamakono pamalo amodzi, mbewu yamakono yopirira ngamba penapo, makololedwe ake safanana ngakhale zochitika paminda yonse zitafanana, adatero Lweya. +Iye adati ngamba ikagwa, mbewu zopirira ngamba zimalimba mpaka kucha ngakhale kuti kucha kwake kumakhala kosafika momwe zingakhalire kutapanda kugwa ngamba. +Iyi ndiyo akuitcha inshulansi kwa mlimi chifukwa zingavute maka amakhala ndi chiyembekezo chokolola kangachepe kusiyana ndi momwe zingakhalire mlimi atabzala mbewu yosapirira ngamba. +Chomwe tikutanthauza nchakuti mlimi azibzala ndi chikhulupiriro chakuti pavute, pasavute adzakolola pantchito yomwe adagwira chifukwa polowetsa paliponse munthu umayembekezera zipatso. +Nzowawa kuti munthu waononga ndalama, mphamvu ndi nthawi yako, pamapeto pake nkudzangopeza misinde yokhayokha popanda chimanga ngakhale chimodzi, adatero Lweya. +Mkulu woyendetsa polojekitiyi, yomwe akuitcha Malawi Improved Seed Scaling Technologies (MISST), Willie Kalumula, adati mbewu zamakono zopilira ngamba zilimo kale mdziko muno ndipo cholinga cha polojekitiyi ndi kulimbikitsa alimi kubzala mbewuzi. +Iye adati cholinga china cha polojekitiyi nkupititsa patsogolo kupekeza ndi kagwiritsidwe ntchito ka mbewuzi, zomwe zikufika kumene pamsika ndi kulimbikitsa njira zamakono za malimidwe. +Kulima mbewu zimenezi kuli ndi ubwino waukulu kwambiri. Akatswiri adachita kafukufuku ndi kupeza kuti mvula ikagwa bwino, mbewu zopirira ngamba zimachita bwino koposa ndipo ikapanda kugwa moyenera mlimi amakololabe ndithu, adatero Kalumula. +Iye adati mbewuzi ndiye yankho lenileni lolimbana ndi njala komanso umphawi ndi kutukula miyoyo ya Amalawi, ntchito yomwe unduna wa zamalimidwe ukugwira. +Chaka chatha, mbewu zambiri zidafota osacha ngamba itagwa mkatikati mwa mvula ndipo alimi ambiri ali pachiopsezo cha njala chaka chino, koma Kalumula adati alimiwa akadabzala mbewu zamakono zopirira ngamba, vutoli silikadaoneka. +Mapemphero a mvula aliko lero Pamene ngamba yadzetsa chikaiko choti Amalawi akhoza kukolola zochepa chaka chino, mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika lero akhala nawo pa mapemphero a mvula amene achitike mumzinda wa Lilongwe. +Malinga ndi mlangizi wa Mutharika pa za chipembedzo Timothy Khoviwa, mapempherowo akhalanso othokoza Mulungu pa zochitika za chaka chatha. +Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mutharika led Malawians in prayer Mapempherowo akachitikira ku Bingu International Conference Centre (BICC) pansi pa mfundo yaikulu yakuti Kudzipereka kwa Mulungu posinkhasinkha mtendere ndi chitukuko cha dziko. +Tikakhalanso tikupempha Mulungu kuti atipatse zokolola zokwanira mu 2016. Kuli atsogoleri a mipingo yosiyanasiyana. Iyinso ndi nthawi yakuti a zipembedzo zosiyanasiyana akhalire pamodzi, adatero Khoviwa. +Mapempherowa akudza pomwe nthambi yoona za nyengo idati kudula kwa mvula kwa sabata ziwiri kwadzetsa chikaiko pakati pa alimi ndi Amalawi ena onse. +Mneneri wa nthambiyo Ellina Kululanga adati kudulaku kwadza chifukwa cha nyengo ya El Nino imene ikuchititsa kuti madera a mchigawo cha kumwera mugwe ngamba pomwe kumpoto ndi pakati chiyembekezo chilipo kuti mvulayi igwa bwino. +Malinga ndi kafukufuku wa nyuzipepala ya The Nation, madera ambiri mvula siyikugwa bwino zimene zingachititse kuti zokolola zichepe. Izi zikudza pomwe mchaka cha 2015 zokolola zidatsika ndi makilogalamu 30 pa makilogalamu 100 alionse chifukwa cha vuto la madzi osefukira amene adakokolola mbewu zambiri. +Msika wa fodya wa okushoni ukuponderezedwa Kampani yoyendetsa malonda a fodya pamsika wa okoshoni ya AHL Group yauza alimi kuti akhale tcheru pogulitsa fodya wawo pa mgwirizano ati kaamba koti cholinga cha ogula fodyawa chokola alimi muukonde wa mgwirizano kuti mtsogolumu alimiwa adzakhale opanda liwu pafodya wawo. +Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mkulu wa zamalonda kukampaniyi Moses Yakobe adauza alimi a fodya ku Lufita, mboma la Chitipa Lachiwiri kuti cholinga cha kampani zogula fodya nkuthetsa msika wa okushoni poika alimi onse pa mgwirizano. +Msika wa fodya wa okushoni Tikasiyanitsa Malawi ndi maiko oyandikana nawo monga Mozambique komwe kulibe okushoni, alimi kumeneko akuvutika chifukwa ogula fodya ndi womwe ali ndi ulamuliro onse; osati olima fodya, Yakobe adatero. +Iye adati izi zaonekera pamsika wa fodya wa bale chaka chino pomwe alimi omwe adatenga ngongole kukampani zogula adagulidwa pamtengo wabwino wa $1.79 (pafupifupi K700). +Yakobe adati alimi omwe adali pa mgwirizano koma sadatenge ngongole adagulitsa pamtengo wa $1.64 ndipo zidavutiratu pa okushoni pomwe fodya adagulidwa pa mtengo wotsikitsitsa wa $1.46. +Polongosola ogulawo adati alimi omwe adatenga ngongole adagulidwa fodya wawo pamtengo wokwererapo kuti apereke ngongole msanga. +Apa chidakula ndikukondera popeza alimi enawanso adakatenga ngongole paokha ena adafufuza ndalama paokha. Koma pano akugulitsa fodya wawo pamtengo wotsika zedi chifukwa choti sadatenge ngongole ku kampani zogula fodya, Yakobe adatero. +Izi zili chonchi, mkulu wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) Alfred Kapichira-Banda wapempha boma kuti lithetse chilinganizochi chimene chidayamba mu 2012. +Tidali maneba ku Gulliver Mawu akuti mbuzi imadya pomwe aimangilira amamveka achabe koma nthawi zina mawuomwewa amakhala ndi tanthauzo lopambana, maka potengera zipatso zomwe abala panthawiyo. +Pachiyambi, Kingsley Blessings Chowawa ndi Loness Gwazanga adali maneba chabe, koma pano chinebacho chawachitira ubwino chifukwa chifukwa chabala chipatso chokoma chomwe awiriwa adzakhale akuchibwekera. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Kunyadirana maneba: Ukwati wa Loness ndi Kingsley udzakhalako pa 3 October chaka chino Awiriwa akuti kukumana kwawo ku Gulliver ku Area 49 nku Lilongwe kudali ngati kwa masewera poti zimaoneka ngati kuyandikana ndiko kumawakokera kufupi ndipo zimaonekanso ngati masewera chabe. +Ineyo ndinkakana chifukwa ndinkati munthu wamkhonde zoona? Mwina angochitira kuti poti ndayandikira mpakana zaka zisanu akundivutitsa kufikira mchaka cha 2011 pomwe ndidamuvomera, adatero Loness, yemwe pano ndi mtolankhani wa Malawi News Agency. +Iye adati atakumana koyamba mchaka cha 2006 sizimamukhudza mumtima ndipo adalibe naye chidwi, koma chifukwa chake mpaka lero sachidziwa. +Iye adaonjeza kuti mokakamiza adayamba kucheza ndipo Kinsley adamufunsira koma iye adakana ndipo akuti mnyamatayu sadagonje ndipo mmalo mwake machezawo adawathamangitsira ku chinzake kuti mwina azichitirana manyazi koma mnyamata sadaimve. +Zitatheka mchaka cha 2011 awiriwa sadafune za bobobo, koma kukaonekera kwa makolo mpaka chinkhoswe chidachitika pa 4 April chaka chino kuholo ya patchalitchi cha Kagwa Woyera ku Area 49 ndipo akuti ukwati woyera udzakhalako pa 3 October ku Chikuti CCAP ku Area 49 komweko ndipo madyerero adzakhala ku Cherub Private School ku Area 47. +Kingsley akuonetsa kuti za msungwanayu adafa mutu koopsa chifukwa adachita kunenetsa kuti azimugwiritsa ngati tambula yagalasi kuopa kuswa. +Chomwe wavutikira chimafunika kusamala kwambiri chifukwa chikatayika ululu wake umakhala waukulu zedi kusiyana ndi chomwe changobwera chokha. Uyu ndiye ndidasankha padziko lonse, adatero Kingsley. +Awiriwa akuti ngakhale kuti banja si msewu wamaluwamaluwa, iwowa adzayesetsa kuti banja lawo lokha lidzakhale loyenda mkuwala ndi lochititsa kaso pamaso pa mulungu ndi anthu. +Kingsley amachokera mmudzi mwa Malembo kwa T/A Khongoni ku Lilongwe ndipo akugwira ntchito kubanki yobwereketsa ndalama ya Select Financial Services, pomwe Loness amachokera mmudzi mwa Kamonga, T/A Kaphuka ku Dedza. +Ulangizi wabala mwana ku Mulanje Njala yomwe yakhudza madera ambiri ikuvutanso mboma la Mulanje komwe anthu akuyembekezereka kutuwa chifukwa cha mvula yanjomba yomwe adalandira nyengo ya mvula yapitayi. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ngakhale njalayi yapereka mantha kwa ambiri, anthu a ku Mulanje West kwa T/A Juma, galu wakudayu wayamba kulambalala chifukwa cha ulimi wamthirira omwe wabonga kumeneko. +Mlimi kupatutsa madzi mmunda wa chimanga Monga akufotokozera Esther Makweya wa mmudzi mwa Mlapa, langizo la alangizi awo ndilo labala zotsatira zabwino kumeneko. Alangiziwo akuti adawauza kuti akumbe zitsime ndi kuyamba ulimi wa mthirira zomwe zabereka mwana. Pano kuderali chimanga chili mbwee pamene ena akubzala, ena akukolola ndipo enanso atangwanika pamsika kukagulitsa chachiwisi. +Aggrey Kamanga ndiye wachiwiri kwa wokonza za mapulogalamu ku nthambi ya zamalimidwe ya Blantyre Agriculture Development Division (Bladd). +Iye adati nkhawa apachika kuti anthuwa angatuwe ndi njala chifukwa chomvera malangizo abwino. +Tidawalangiza kuti ayambepo ulimi wa mthirira pokumba zitsime komanso pafupi ndi iwo pali mtsinje womwe suphwerapo. Pano aliyense ali kalikiliki ndi ulimi pamene ena tawalangiza kuti ayambiretu kupanga manyowa, adatero Kamanga. +Mavuto a madzi akula mu October ku Lilongwe Pomwe anthu mumzinda wa Lilongwe akubangula ndi vuto la kuzimazima kwa magetsi, kampani yopereka madzi ya Lilongwe Water Board yachenjeza kuti madzi nawo avuta mwezi ukudzawu. +Mneneri wa bungweli, Bright Sonani, watsimikiza za nkhaniyi koma wati anthu asade nkhawa kwambiri chifukwa madzi azitulukabe ngakhale mwa apo ndi apo. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Sonani wati bungweli litulutsa ndondomeko ya mmene madzi azitulukira kuti anthu azitunga nkusunga madzi okwanira mmakomo mwawo panthawiyi. +Mwezi umenewu tikhala tikukonza ena mwa mathanki omwe timasungiramo madzi. Tikuchita izi malingana ndi kuti anthu ogwiritsa ntchito madzi akuchuluka ndiye tikufuna kukhala ndi mosungira mokwanira, adatero Sonani. +Malingana ndi chikalata chomwe bungweli lasindikiza, madzi azidzasiya 6 koloko mmawa ndi kuyambanso kutuluka 6 koloko madzulo ndipo tsiku loyamba kusiya ndi Lolemba pa 28 September. +Potsirapo ndemanga, wapampando wa mabungwe a anthu ogwiritsa ntchito madzi mumzinda wa Lilongwe, Bentry Nkhata, wati nkhaniyi ndi yoopsa polingalira kuti anthu amadalira madzi pamoyo wawo wa tsiku ndi tsiku. +Iye adati madzi akasowa matenda, makamaka ammimba monga kolera ndi kamwazi, amabuka kaamba koti anthu amamwa ndi kugwiritsa ntchito madzi osatetezedwa. +Nkhani yowonjezera mosungira madziyo ndi yabwino chifukwa zikutanthauza kuti mtsogolo muno madzi sazidzavutavuta koma nkhawa ili pakuti anthu azigwiritsa ntchito chiyani? Nthawi zambiri madzi akasowa kumakhala mavuto aakulu, adatero Nkhata. +Unduna wa zaumoyo wati nkhaniyi isachititse anthu kutayirira ndipo wati chofunika nkusunga madzi okwanira mmakomo mwawo kapena kugwiritsa ntchito njira zotetezera madzi. +Pafupifupi mdera liilonse muli alangizi a zaumoyo choncho tiyeni tonse tiziwafunsa momwe tingatetezere madzi kuti tipewe matenda ammimba panyengoyi, adatero mneneri wa unduna wa zaumoyo, Adrian Chikumbe. +Nthawi zambiri madzi akasowa, anthu amadalira zitsime kapena mitsinje yomwe madzi ake amakhala ndi dothi komanso tizilombo toyambitsa matenda ammimba. +Abusa ku HIH ndi zina Tsikulo ndidali pa Wenela kuitanira minibasi monga mwanthawi zonse. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ndirande iyi! Machinjiri iyo! A Lilongwe achamba atatu iyo yopita! Ndati achangu atatu a Lilongwe iyi! Mukudziwa kale. +Nthawi imeneyo nkuti ndikumveratu nyimbo zatsopano zokhazokha, ma headphone ali kukhutu. Pamaphulikatu nyimbo zongomasula kumene: Namadingo adabwera ndi Msati Mseke, Wambali amvekere Asungwana a kwa Chitedze, anyamata a ku Chileka akuti Mr Bossman ndipo Lucius akuti Walema. Osaiwala munthu wamkulu Nkasa akufwamphula Anenere. +Ndidachotsa ma headphone mkulu wina atandikodola. Iyetu adali atangotsika basi ndipo ndidadziwiratu kuti ndi mbusa. +Musandifunse kuti ndidadziwa bwanji chifukwa sindikuyankhani. Ndipo nkakuuzani kuti ndidaonera mwinjiro wake wakuda, ndi kolala yoyera muchitapo chiyani? Nanga nkakuuzaninso kuti simukudziwa kolala yoyerayi idabwera bwanji mulephera kuyankha. +Ndangokhala muno muliyenda kuchoka kwathu kwa Kanduku komwe ndidasiya mkazi wanga wokondeka, Nambe, koma ndimadziwa kuti nthawi imeneyo abusa ankaphedwa pochekedwa makosi. Iyitu idali nthawi yowawitsa pamene kukhala mbusa chidali chinthu choopsa zedi. Komatu abusa anthawiyo adali olimba mtima ndipo adayamba kuika kolala yoyera pakhosi kuti langa ndi limeneli liduleni koma sindisiya kufalitsa uthenga wabwino, kuthandiza kuti ochimwa asinthe ndipo iwo ali olungama apitirize kutero. +Ameni? Atsogoleri, inetu wanga ndi wa ku HIH, ndikwere ya chiyani? adandifunsa. +Ya Ndirande, kapena ya Machinjiri. Kwerani iyi abusa. Ya Machinjiri ndi K200, ya Ndirande K100. Simufuna bodyguard? Ndikumvatu kwaterera, ndidatero. +Adangoseka, uku akukwera minibasi ya Ndirande. Akukwera, ndidaona chisenga chikusuzumira. +Madzulo a tsikulo, tili malo aja timakonda pa Wenela, adatulukira Abiti Patuma ali wefuwefu. +Mkulu wina wandilipirira kuti ndipeze chitupa choyendetsera galimoto. Koma eeeh! Abale ku Ginnery Corner uku kuli gahena ndithu. Kudikira tsiku lonse uli chiimirire koma chitupa osatuluka, adalira. +Bwanjinso nanga? ndidafunsa. +Kuli mazunzo. Ena akundiuza ayendera masiku 8 nkhani yomweyi. Ukapolotu uwu. Tsono nthawi yotakata mtaunimu ikhalapo? Ndalama zopereka ndiye simasewera. Akatolera ndalamazo ndiye basi kususa kukhalepo. Osololawo aiwala kuti lero Adona Hilida athawa pano pa Wenela kuopa kukwizingidwa poti ena akuti akukhudzidwa ndi kusolola mopanda manyazi kudagundika ku Kapitolo, adatero Abiti Patuma. +Palibe icho ndidatolapo. +Mwati chiyani? adafunsa wapamalopo, Gervazzio. +Kodi simunamve kuti Mani Rich alembera akatalangwe ena kuti Adona Hilida akusautsidwa mmaganizo ndi anthu amene akusaka moyo wawo? Nanga simunamvenso kuti uja wa mabasi Leo wachita muja adachitira Pitapo, kunena kuti Adona Hilida ndiwo adawatuma kusolola khobidi? adayankha Abiti Patuma. +Tonse tidangoti kukamwa yasaa! Man Rich amafatsa! Atatsegula wailesi Gervazzio, tidangomva mkulu uja adawerenga kwambiri vesi yaifupi mbaibulo akulankhula. Mwamuiwala kale mkuluyu? Nanga ndichite kukuuzani za vesi ija imati Yesu analira? Kapena mwamuiwala mkulu woyanganira maula adalira pomwe adanena kuti Moya Pete ndi Dizilo Petulo Palibe ndiwo akadaulo pobera maula? Amene apambana ndi Dizilo Petulo Palibe, Ukafuna Dilu Fatsa komanso Male Chauvinist Pigs, adatero mkuluyo. +Posakhalitsa adatulukira Kenny Foot Soldier Nsongo. Atiberanso maula. Panalibe chilungamo pamaula amenewa. Pali kukondera, adali kutero. +Shhhhh! Tikumvera nkhani. Mipingo ina idzatha ngati makatani, adatero Abiti Patuma. +Mlaliki wozizwitsa pa Wenela Tsikulo pa Wenela padali mapemphero. Abale anzanga kwadzatu alaliki. Koma ine sindiiwala ntchito za ulaliki za Shadreck Wame amene adatipezapo kwathu kuja kwa Kanduku. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Iyetu palibe tsiku ndi limodzi lomwe limene adayesera kusandutsa miyala kukhala masikono. Palibe tsiku ngakhale limodzi limene adayerekeza kunena kuti akhoza kuchita zozizwitsa posandutsa atate wawo kukhala mayi wawo. +Ndikumbuka ulaliki wa mlaliki wa ku Mdikayo pomwe adafika kwathu kwa Kanduku. Adalumikiza malembo oyera ndi nthano yake. +Padali fisi yemwe adaona mayi wina akuyenda atasenza dengu lake. Mayiyo amati akamayenda, amagwedeza mkono wake. Fisi adayamba kutsatira mayiyo poganiza kuti mdengu mudali nyama yochuluka. Ndipo poona mkonowo ukuyenda kupita kutsogolo, kumbuyo, kutsogolo, kumbuyo, fisi adali kutsatira. +Mumtima adali kunena igwa ntola. Mayi adaoloka mitsinje, fisi pambuyo amvekere: igwa ntola. Mayi adatsika zidikha, fisi pambuyo ali: igwa ntola. +Mayi adakwera mapiri, kutsika mapiri, fisi pambuyo: igwa ntola. +Uwutu udali ulaliki wogwira mtima chifukwa fisiyo adatsatira mayiyo, koma nyama osagwa. Mapeto ake, fisi adafa ndi njala komanso kutopa. +Izitu ndidakumbukira chifukwa cha mapemphero adali pa Wenelapo. Kudali mwana wa munthu ndipo mumtima ndidati: Awa kutengeka ngati fisi. Igwa ntola. +Alleluya! Idzani kwa ine nonse osauka mudzachita bwino. Bwerani kwa ine akuchita kusaweruzika ndifufute machimo anu ndi labala uyu! Inde nonse ochita chigololo ndikukhululukirani. Muone lero mirakuli, adatero wolalikayo. +Adali wamfupi, koma momwe adayambira kutalika! Adatalika, kutalika mpaka mutu wake udasowa mmitambo. Tonse tidazizwa. +Posakhalitsa adabwerera mukufupika kwake. +Ndaona ndithu zobwera mawa mmitambomo. Ndaona kuti njala yonse itha ndipo Moya Pete palibe awachitirenso nsanje chifukwa chotenga abale awo onse kukaonera kukumana kwa Omaba ndi Papa ku Orleans. Inde, ndaona mankhwala azitsamba akupezeka ponseponse anthu kusiyanso kudalira zipatala zopanda aspirin. +Inde, ndaona mitengo ya zinthu ikutsika mochititsa chidwi komanso ndaona Lazalo Chatsika akutsutsa molimbika zolakwa za Moya Pete. Komanso ndaona madzi, magetsi zikusefukira pano pa Wenela ngati madzi a mu Shire, adapitiriza. +Akutero nkuti akuseweretsa foni yake yammanja. Idalitu mose walero. +Kuti tikhululupirire kuti si zadziko lapansi mukuchitazi, jambulani chithunzi pogwiritsa ntchito kafoni kanuko, adatero Abiti Patuma. +Indetu indetu ndinena ndi iwe Patuma Didimo. Ndimakudziwa! Nanga dzina lako ndalitenga kuti? adafunsa mlaliki. +Ndidazizwa naye. +Akulu, mwaiwala mudandionetsa chipsera chili pamsana panu tsiku lina mnyumba yogona alendo ija? Jambulani chithunzi ndi foni yanuyo basi, adayankha. +Mlaliki uja adaimika foni yake nkuyamba kujambula mlengalenga ndi kafoni kake. Adationetsa chithunzi chomwe adajambulacho. +Padali nkhope ya mkulu uja wotchuka, Fula Kasamba. +Aaaargh! Ukutionetsa Fula, kodi si mnzako ameneyo? Udajambula kalekale chithunzi chimenecho. Zanu nzimodzi, adatero Abiti Patuma. +Komanso uyo Fula ukuti wajambulayo ali kozizira ati chifukwa adati woweruza ndi Alice in Wonderland. Izi akuti adazitenga pa Yobu 13:11, ndidatero. +Koma akadadziwa! Mkulu uja adachita ngati akuuluka, nkuyamba kuyenda mmalere. +Indetu, ndinena ndi inu akusowa chikhulupiriro. Kodi iye wakuyenda pamadzi ndi iye wakuyenda mumlengalenga, wamphamvu ndani? adafunsa. +Abale anzanga, apa mpomwe ndidadzidzimuka kumalotowo. +Umhlangano wa Maseko Ngoni lero Kutentha masanawa kumanda kwa Gomani kwa Nkolimbo mboma la Ntcheu pamene Angoni a mmaiko monga Zambia, Mozambique, Tanzania, South Africa komanso Swaziland akhale akukumana pamwambo wachikhalidwe. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Umhlangano ndi mwambo wa Angoni umene pamakhala magule komanso miyambo ina monga kuulutsa nkhunda yoyera ndi kukhwisula. +Inkosi ya Makhosi Gomani Wachisanu pocheza ndi Tamvani lachitatu yati zokonzekera zonse zatheka kuti mwambowu uchitike lero ndipo anthu ochokera mmadera ena adayamba kufika kumaloku Lachiwiri. +Pamwambo wokhwisula anthu amasonkhana mmawa ndipo amakayendera pamene adagona Chikuse Gomani l. Chikuse ndiye mfumu yoyamba ya Angoni a kwa Maseko imene idaphedwa ndi azungu chifukwa chomenyera ufulu wa anthu akuda. +Pamandapo pamakhala mapemphero komanso mwambo wopempha madalitso ndipo mfumu yaikulu ya Angoni a kwa Maseko ndiyo imatsogolera mwambowo. +Apapa ndiye kuti wotsogolera mwambowu ndineyo. Pamwambowu amayi samakhalapo. Mwambo umenewu ndiwo umayambirira kuchitika ndipo uchitika nthawi ikamati 5 koloko mmawa, adatero Gomani V. +Iye adati pamwambowu pakakhalanso mwambo woulutsa nkhunda zoyera. +Kuulutsa nkhunda kumatanthauza mtendere. Angoni timalimbikitsa mtendere ndiye pamwambowu timaulutsa nkhunda zoyera zomwe [zikuimira] mtendere, adaonjeza. +Mwambo wa chaka chino wakumana ndi zovuta zingapo monga kumwalira kwa Inkosi Phambala komanso Bvumbwe. +Gomani adati iyi ndi nkhani yachisoni ndipo pakakhalanso nthawi yokumbukira mafumuwa, omwe adati adali mafumu okonda ndi olimbikitsa chitukuko mmadera awo. +Zovala ndi zakudya Zachingoni ziyalidwa kuti anthu akasirire komanso kugula. Gomani adatinso ngakhale mwambowu ndi Wachingoni, anthu amitundu yonse akuitanidwa kuti adzasangalale nawo limodzi. +Ngoma, uyeni, nkhwendo ndi msindo ndi ena mwa magule amene asangalatse anthu obwera kumwambowu, adatero Gomani. +Mswati adakali mfumuBoma Boma, kudzera mwa mneneri wa unduna wa maboma aangono ke Muhlabase Mughogho, lati ngakhale pali kukokanakokana pa ufumu wa Gomani V, boma likuvomerezabe Mswati Gomani wachisanu kuti ndiye mfumu. +Mughogho adanena izi pamene mbali ina ya banja la Gomani motsogozedwa ndi Dingiswayo yalengeza kuti Dingiswayo ndiye mfumu, kulanda ufumuwu kwa Mswati. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Gomani V Lachiwiri akuluakulu ena abanja adatsutsa zomwe Dingiswayo adalengeza kuti Mswati adakalibe mfumu. Koma patangodutsa tsiku abanjawa atalankhula, Dingiswayo adachititsanso msonkhano wa atolankhani kuti zomwe adanena abanjawa ndizabodza ndipo iye ndiye mfumu yatsopano. +Panopa ofesi ya Gomani yasamuka kuchoka ku Lizulu ndipo tikulankhulamu ili kwa Nkolimbo, adatero Dingiswayo. +Koma malinga ndi Mughogho, Mswati ndiye mfumu. Boma likudziwa Mswati kuti ndiye mfumu, izi zili choncho chifukwa mfumu ikasankhidwa ndi abanja, boma limavomereza ndipo mwambo udachitika wodzoza Mswati kukhala Gomani wachisanu. Izi sizidasinthe mpaka lero. +Gawo 11 (1) la malamulo okhudza mafumu, Chiefs Act la mchaka cha 2000 limati pulezidenti wa dziko ndiye ali ndi mphamvu yochotsa Paramount Chief, Senior Chief, Chief komanso Sub Chief. +Mswati adadzozedwa mu pa August 10, 2012 kukhala Gomani wachisanu kutsatira imfa ya bambo ake. +Zulani mitengo ya fodya poopetsa matenda Nthawi ino alimi ambiri a fodya ali kalikiriki kufunafuna mbewu, kukonza malo omwe adzalimepo komanso kukonza ndi kufesa nazale. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ngakhale izi zili choncho alimi ena mmaboma a Mzimba ndi Rumphi akutsalira pantchitoyi kaamba koti iwo sadazulebe mitengo ya fodya mminda mwawo. +Mlangizi wa za ulimi Lewick Zimba wauza Uchikumbe kuti izi zikhoza kudzaononga fodya munyengo ikubwerayi. +Alimi amayenera kuzula ndi kuotcha mitengo imeneyi akangomaliza kuthyola fodya wawo kuti aphe tizilombo tonse tomwe tingakhale mumitengoyo. +Fodya ali gulu limodzi ndi tomato ndi mbewu zina zomwe sizichedwa kugwidwa ndi matenda ndipo mitengo ija ikasiyidwa kwa nthawi yaitali mmunda umasanduka malo omwe tizilombo timasweranamo,adatero Zimba. +Zimba adati madera amasiyana nyengo yokolola fodya. Madera a kummwera ndi pakati amayenera kuyambirira kuzula pomwe madera a kumpoto amamalizira ngakhale nthawi yake madera onsewa ndi miyezi ya March mpaka April, adatero Zimba. +Iye adati alimi omwe sadazule ndi kuotcha mitengo ya fodya mminda mwawo akuyenra kutero nthawi ino ngati akufuna kudzapindula ndi fodya wawo nyengo ikudzayi. +Fodya amafunika chisamaliro chokwanira ndipo chisamaliro chimenechi chimayamba mlimi akangokolola fodya wake mmunda, adatero Zimba. +Iye adati alimi akuyenera kuzindikira zomwe akuyenera kuchita ndi nthawi yomwe akuyenera kutero kupewa kulakwitsa kapena kusokoneza zomwe zikadatha kupeweka. +Alimi akuyenera kumvera alangizi komanso ngati apali zinthu zomwe sakumvetsetsa akuyenera kufunsa kwa alingizi a kudera lawo, iye adatero. +Mlangiziyu adati Malawi ndi dziko lomwe limadalira ulimi wa fodya pobweretsa ndalama za kumaiko akunja kotero nkofunika kuti fodya azisamalidwa bwino kuti phindu lake lizioneka pokhala kuti mbewuyi imafuna ntchito yambiri. +Amon Gondwe, mmodzi mwa alimi amene mpaka pano sanazulebe mitengo ya fodya mboma la Rumphi, wati ntchito imawakulira kuti ayambe kuzula nthawi yomwe amaliza kuthyola fodya. +Timati tidzazulabe kenaka mpaka kumapezeka kuti nthaka yauma ndipo mitengoyi imalimba ndiye timangozisiya, adatero Gondwe. +Iye adati akudziwa za ubwino wozula mitego ya fodyayo akangomaliza kukolola, makamaka potengera kuti ntchito imachepa, koma kwina kumakhala kutayirira kumbali ya alimi, amene ambiri mwa iwo amafuna adzipepese kaye akangogulitsa fodya wawo. +Zefinati Alick: Kadaulo posema ziboliboli Aluso ndi onse koma luso losema ziboliboli si lachibwana, limafunika khama komanso munthu wolimba mtima. Pa Golomoti mboma la Dedza pali malo otchedwa Golomoti Curios Group amene amapanga ndi kugulitsa ziboliboli. Zefinati Alick nthawi zonse amakhala pamalopa kugulitsa katundu wake uku akupanga wina. BOBBY KABANGO adacheza naye za luso lake motere: Tidziwane wawa Ndine Zefinati Alick, ano ndi malo anga koma zones ndikupangira limodzi ndi mkulu wanga amenenso adandiphunzitsa ntchitoyi. +Alick ndi ziboliboli zake Kodi malo ano adatsekulidwa liti? Adatsekulidwa mu 2012, koma ineyo ndidayamba kusema ziboliboli mu 1998. Panthawiyo ndinkagwirira ntchitoyi ku Mua kenaka ndinkapangira kunyumba kwanga. Mu 2012 mpamene timatsekula malo ano. +Ndi zinthu ziti mumasema? Timasema mtundu ulionse wa zinyama womwe munthu akufuna, chifaniziro cha munthu, Mayi Maria, chifaniziro cha anthu amtundu Wachingoni, galimoto ndi zina zambiri zomwe sindingakwanitse kuzitchula. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Mukugwiritsira ntchito mtengo wanji? Pali mitengo yambiri yomwe anthu amagwiritsira ntchito koma ife timakonda mtengo wa mtumbu. +Mumagwiritsira zida ziti popanga katunduyu? Mukakadula mtengowo, mumayenera muyambe kusema ndi sompho, chikwanjenso chimafunika, tchizulo, sandpaper, polishi ndi zida zina ndi zina kuti chomwe tikusemacho chioneke bwino. +Kodi chomwe mwanyamulacho nchiyani? Nanga zimatenga masiku angati kuti ntchito itheke? Mutiuzenso mitengo yake Ichi ndi chifaniziro cha nyama ya chipembere. Chimatenga sabata ziwiri mwina osafikanso malinga ndi nthawi yomwe uli nayo kuti chithe. Chimenechi chikugulitsidwa K10 000. Chinachi ndi chifaniziro cha mayi Wachingoni. Ameneyu amatha mofanana ndi chinyamachi bola ukhale ndi nthawi. Mayiyu timagulitsa K15 000. +Mwathandizika bwanji ndi ntchitoyi? Ndagula nyumba, ndimalipirira ana sukulu komanso feteleza ndimagula kuchokera ntchitoyi. Ndipezereponso mwayi kuwauza anthu kuti ife timapanga chilichonse chomwe akufuna, komanso momwe akufuna chionekere. +Tidangoonana koyamba basi Kukumana kudziko la eni nkudziwana kuti mumachokera kumodzi ndi chinthu chonyaditsa kwambiri moti kwa anthu ena chinansi chimayambira pomwepo ngakhale atakhala kuti amachokera mzigawo zosiyana kwawoko. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Nkhani yathu lero ndi ya Wonder Msiska, wochokera mboma la Karonga yemwe akugwira ntchito kuwayilesi ya Staryomwe idaphathikana ndi kanema ya Timveniyemwe pano ali pabanja ndi Hazel Silekile, naye wa ku Karonga, ndipo akugwira ntchito kukampani ya BETAMS Ltd. +Sadzalekana: Wonder ndi Hazel kutsimikiza kuti ali thupi limodzi Awiriwa adakumana ku Britain mchaka cha 2008 komwe onse adapitira maphunziro ndipo adakaphana maso kumwambo wa chinkhoswe cha Mmalawi wina wake nkukondana pomwepo. +Zidangochitika kuti takondana basi. Ndikhulupirira ndi momwe Mulungu adakonzera. Choyamba, tonse tidapitira maphunziro kenako nkuganiza zopita kumwambo wa chinkhoswe komwe tidakakumana, adatero Wonder. +Iye adati atakumana kuchinkhosweko sipadatenge nthawi kuti ubwenzi uyambe mpaka kugwirizana za banja komweko. +Kusiyana ndi ena omwe amadikira tchuthi kuti akapange chinkhoswe kwawo, Wonder ndi Hazel akuti chinkhoswe chawo chidachitikira ku Mangalande komweko ku Sutton Coldfied mchaka cha 2009. +Si kuti udali mwano kapena kudzitama, ayi, koma tinkafuna kuti timaliziretu zomwe tidapitira kumeneko komanso panthawi yomweyo tionetse kuti tidakondanadi. Titabwerera kumudzi ku Malawi mpomwe tidayamba za mwambo waukulu wa ukwati, adatero Wonder. +Ukwati wa awiriwa udachitikira mumzinda wa Blantyre mchaka cha 2012 atabwerako ku Mangalande ndipo pano ali ndi mphatso ya ana aakazi awiri. +Wonder adanenetsa kuti atakhalanso ndi mwayi wina wosankha wachikondi akhoza kubwereza chisankho chake chifukwa iye mtima wake udakhazikika pa Hazel ndipo ndi khumbo lake kudzasungana naye mpakana kalekale. +Hazel adati kwa iye Wonder ndiye mbali imodzi ya thupi lake ndipo sangagwedezeke ndi chilichonse chifukwa mwa iye adapeza mwamuna wachikondi ndi wachilungamo. +Akuti iye akakhala, kaya nkutchito, pakhomo ngakhalenso kunyumba saona chomulekanitsa ndi mwamuna wakeyu ndipo naye ali ndi chiyembekezo cha banja lapamwamba ndi lotsogola komanso latsogolo lowala. +Zilango zophweka zivulaza maalubino Miyezi 18 kwa ofuna kugulitsa alubino ku DZ Pali mantha kuti maalubino angapitirire kuona zokhoma mdziko muno ngati boma silichita machawi kuti lamulo latsopano loteteza anthuwa liyambe kugwira ntchito, mkulu wa bungwe lomenyera ufulu wa maalubino la Association of People with Albinism in Malawi (Apam), Bonface Massah, watero. +Mantha a mkuluyu akudza pamene anthu amene apezeka olakwa pozunza kapena kusowetsa maalubino akupitirira kulandira zilango zozizira. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Lachisanu sabata yatha, bwalo la milandu mboma la Dedza lidagamula mayi Siyireni Nyata ndi Chrissie Lajabu kukaseweza kundende zaka ziwiri ndi miyezi 6 poopseza mwana wa zaka 14 kuti amupezera kale msika. +Malinga ndi mneneri wa polisi ku Dedza, Edward Kabango, amayiwa akhala akulankhula izi kwa nthawi yaitali. +Amati ndi kanyama kosendasenda ndipo akapezera kale msika woti akakagulitse, adatero Kabango. +Kaamba ka kuopsezedwako, mwanayo akuti adasiya sukulu pochita mantha kuti angakumane ndi anthu amene amati amugulawo. Makolo a mwanayu akuti adakadziwitsa apolisi ndipo pa April 15 amayi awiriwo adanjatidwa. +Bwalo lidawapeza olakwa ndipo lidawaimba mlandu wobweretsa mantha kwa mwanayu ndipo adawalamula kuti akaseweze zaka ziwiri ndi miyezi 6 kundende. +Chilangocho chikudza pamene mkulu winaso ku Machinga, Sinoyo Wyson, wagamulidwa kuti akakhale kundende zaka ziwiri posowetsa mwana wa zaka 11 wachialubino. +Mu May chaka chinonso amuna awiri ku Zomba adawalamula kukaseweza miyezi 12 popezeka ndi mafupa alubino. +Massah akuti si zoona kuti milandu yotere izikhala ndi zilango zofewa ndipo wati bungwe lawo lichitapo kanthu kuti maalubino asamakhale mwamantha. +Ndikumvanso kwa inu za nkhani ya ku Dedzayo, koma tifufuza. Pankhani ya ku Machinga ndiye tidakagwadanso kubwalo lalikulu kuti aunikenso chilangochi, adatero Massah. +Koma iye adati oweruza milandu si olakwa pa zigamulo zomwe akuperekazi chifukwa malamulo a dziko lino amapereka zaka ziwiri kwa wopalamula mlandu wozembetsa munthu. +Iye adati mavuto onsewa angathe ngati lamulo la Anti-Human Trafficking lingayambe kugwira ntchito. Lamuloli lidavomerezedwa kale ndi aphungu a Nyumba ya Malamulo komanso mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika. +Lamulo latsopanoli likupereka zaka khumi kwa amene wapalamula mlandu wonga uwu, chomwe ndi chilango chokhwimirako. Tayesera kufunsa anzathu a boma nthawi yomwe lamuloli liyambe kugwira ntchito koma zomwe tikumva si zopereka chiyembekezo. +Maalubino sakutetezedwa kupatula kungolankhula chabe, zomwe sizingateteze anthuwa, adatero Massah. +Koma mneneri muunduna woona za chilungamo ndi malamulo, Apoche Itimu, akuti lamuloli lidavomerezedwa kale ndi Mutharika. +Chomwe ndikudziwa nchakuti lamuloli lidavomerezedwa, sindingakumbuke kuti lidasindikizidwa liti. Panopa kwangotsala kuti liyambe kugwira ntchito, koma ngati mukufuna kudziwa zenizeni za lamuloli funsani unduna wa zamdziko, adatero Itimu pouza Tamvani. +Mneneri ku unduna wa zamdziko, Rose Banda, Lachiwiri msabatayi adati timuimbire tsikulo lisadathe kuti atipatse zenizeni zokhudza lamuloli. +Koma pakutha pa tsikulo Banda adati sadakumane ndi oyenerera amene angamufotokozere nkhani yonse yokhudza lamuloli. +Lachitatu adatitumizira uthenga pafoni kuti akhala ndi zotsatira zonse pofika Lachinayi. +Maiko monga Tanzania, Mozambique, South Africa ndi Zambia ali ndi lamuloli lomwe limakhaulitsa opezeka kuti apalamula mlanduwu, pamene mtsogoleri wa dziko la Zimbabwe Robert Mugabe adakhazikitsa ndondomeko yapadera yothanirana ndi anthuwa. +Mutharika wakhala akumalankhula pawailesi ya MBC mawu oopseza kuti amene apezeke akusautsa maalubino athana nawo. +Koma ngakhale Mutharika angalankhule maka, kukhoti akuyendera zomwe malamulo amanena posatengera mawu ake. Izi zapangitsa mabungwe monga Apam kuti alimbikitse kupempha boma kuti likhazikitse lamulo lokhwima pofuna kuteteza miyoyo ndi maufulu a maalubino. +Massah akuti nthawi yakwana kuti mabungwe amene amamenyera ufulu wachibadwidwe ndi ena agwirane manja pofuna kuthana ndi mchitidwe wozunza maalubino. +Mdziko muno mukangochitika nkhani mumaona amabungwe akubwera pamodzi kudzudzulapo, koma zomwe zikuchitika mmakhoti athu palibe amene akulankhulapo. Tikufunika tigwirane manja kulimbana ndi nkhaniyi ngati tikufuna tipambane nkhondo yoteteza anthu [amene ali ndi zilema monga maalubino], adatero Massah. +Nkhani zosowetsa maalubino komanso kufukula manda awo zidafika pachimake mu February chaka chino ndipo anthuwa pamodzi ndi amabungwe ena adachititsa msonkhano mumzinda wa Blantyre kudandaulira boma kuti lichitepo kanthu. +Pamsonkhanowo, Senior Chief Kawinga ya mboma la Machinga idati ndi zosamveka kuti chilango cha wosowetsa munthu chizikhala chochepa. +Munthu wina adaba ngombe koma adamupatsa chilango choti akakhale kundende zaka zisanu pamene wosowetsa munthu akumupatsa zaka ziwiri. Pali chilungamo apa? Kodi ngombe ikhale yofunikira kwambiri kuposa munthu? Kodi alubino si munthu? adadandaula Kawinga. +Mwambo woliza mfuti pamaliro Achingoni Mfumu Yachingoni ikagona, pamaliropo amaomba mfuti thupi la mfumuyo lilowe mmanda. Mwezi wathawu, kudachitika maliro a T/A Bvumbwe mboma la Thyolo. ku malirokonso kudalizidwa mfuti, chomwe anthu ena amene adali kumwambowo adadabwa nacho. BOBBY KABANGO adacheza ndi mkulu amene amaomba mfutiyo kuti amve zambiri za mwambowu motere: Wawa Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Fikani ndithu musaope. +Ndikudziweni bwanji? Choyamba dzina langa ndine Moses Chikoko. Mungandidziwe monga mbali ya mbumba kwa T/A Bvumbwe. Ngati mudamvapo za Gomani Chikuse amene adadulidwa khosi, ameneyo ndiye adabereka mayi anga. Mkazi wachinayi wa Gomani Chikuse ndi amene adabereka mayi angawo. +Ndiye mudapezeka bwanji kuti mukukhala ku Thyolo kuno? Pajatu Angoni adali ankhondo, ndiye gulu la mayi anga ndi lomwe lidabwera kuno pamene Angoni ena ankafikira madera ena. Mayi anga adali wa mtundu wa Maseko koma bambo anga adali a kwa Mulauzi. +T/A Bvumbwe wagonayu adali ndani wanu? Wagonayu ndi mwana wanga, koma sindikutanthauza kuti ine ndi amene ndidabereka iyeyu, koma kuti bambo ake adayenda limodzi ndi ine kusukulu, amenewo adali a Steven Bvumbwe. +Mfuti mwatengayi mufuna mugwiritsire ntchito yanji? Ngati mukumva kulira mfuti pamalo pano ndikuliza ndineyo, ntchito yake nkuti ilire pamene tikugoneka mfumu yathu. Dziwani kuti pamaliro a mfumu Yachingoni pamalira mfuti mpaka mfumuyo itatsikira mmanda. +Mumaliza kangati? Mfuti imalira kanayi. Koyamba imalira kusonyeza kuti mfumu yamwalira. Apa amakhala kuti amene alowe mmalo mwake wabwera kudzaona nkhope ndi kutsimikizadi kuti mfumuyo yamwalira. Imalira kachiwiri pamene tikutulutsa thupi la mfumuyo mnyumba. Timalizanso kachitatu pamene tanyamula thupi ulendo kumanda. Pamenepa timaomba kusonyeza kuti akutsanzika. Timadzaombanso komaliza pamene bokosi latsitsiridwa mmanda kusonyeza kuti wafika. +Chifukwa chiyani mumaomba mfuti? Kusonyeza kuti Mngoni ndi wankhondo. Ndiye ngati Mngoni, yemwe timamudziwa bwino kuti ndi wankhondo, wamwalira zotere zimayenera zichitike. +Bvumbwe adamenya kuti nkhondo yake? Bvumbwe adali Mngoni ndipo Angoni amadziwika kuti ndi ankhondo ngakhale sadamenye nkhondoyo. Sindingakuyankheni kuti adamenya kuti koma dziwani kuti Bvumbwe adali Mngoni yemwe ndi wankhondo. +Nkhondo yake iti kodi? Mukudziwa kuti Angoni adachita kumenya nkhondo mpaka kudutsa ku Domwe. Akafika pamalo amayamba amenya nkhondo ndi kukhazikika bwino. Nkhondo yake ndi imeneyo. +Kodi ndimayesa nkhondoyo idatha kalekale? Nanga inu mukuchitabe izi bwanji? Eya, koma nkhondo yathu ndi ya mmagazi, kusonyeza kuti simatha. Mwambo umenewu udayamba kalekale ndi makolo athuwo. +Mfuti zisadayambe kupangidwa mumaliza chiyani? Aaah, mwaiwala? Kudali mfuti zagogodera zomwe tinkagwiritsa ntchito nthawi ngati ino. +Mwapeza bwanji chilolezo choliza mfuti? Choyamba dziwani kuti ndine msirikali, mfuti ndimaidziwa chifukwa cha ntchito. Ndilinso ndi mfuti komanso ndidali Wapayoniya. Ndiye mnyumba mwanga mfuti si yachilendo. +Anthu enatu amadzidzimuka, mumakhala ndi chilolezo kuti muombe mfuti? Nchifukwa chake mwandiona kuti ndakhala kutchire ndekhandekha podziwa kuti pali anthu odwala mtima amene angathe kukomoka mfuti ikalira. +Ndiyetu tailozetsani kumbali kuopa kuti chipolopolo chingafwanthuke Ndikudziwa chomwe ndikuchita, apapa olo zitachita kuvuta kotani singalire. +Ntchito za Kumbu Kalipo (KK) Tsikulo pa Wenela padaterera ndithu. Aliyense adali ndi chodzala tsaya chimwemwe. Sindikudziwa kuti zidali choncho chifukwa chiyani. +Komatu ngakhale kudali chimwemwe chotero, inetu msunamo udali kuno. Ndidali kudandaula chifukwa mmodzi mwa anthu amene adandilandira pano pa Wenela adali atatsamira mkono. Iyetu ndi amene nthawi ina ankandiphunzitsa kukonza galimoto. Ndipo tsiku lomaliza, adandiuza ndikamuthandize kukonza galimoto kuti tikaone zina uko kwa Edgar Lungu, mtsogoleri wothamanga. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Lero wapita. +Pajatu ati moto umapita kwatsala tchire. Pamene tikuyembekeza kuti iye akhale mchiyero, malingaliro ali pa ife otsala. +Ause ndi mtendere. +Choncho, monga ndanena kale, chimwemwe chidali pa Wenela inetu sichinkandikhudza. Koma ndidazizwa atatulukira KK, inde Kumbukani Kalipo, sikanathe. +Nonse amene mumachokera ku Northern Republic, inde Nyika Province, nthawi yanu yakwana. Tipeza mipando ndipo onse obulumunya maswiti polankhula, okazinga chimanga, nthawi yawo yatha kwambiri. Ndabwerera, adatero Kumbu. +Abale anzanga, ngati ndidatolapo kanthu? Nthawi yanu idatha. Ngakhale muyese izi ndi izo, zanu zidada basi, adatero Abiti Patuma. +Adandikulunga mmasamba ansatsi. +Usatero mwaiwe. Ukudziwa Adona Hilida akabwera kumakhala mpungwepungwe. Anabweratu ndipo tagwirizana zosadabuza zinthu pano pa Wenela, adayankha Kumbu. +Mwinatu muli ngati mkazi wanga Nambe kuti simudziwa umo zinthu zikuyendera pano pa Wenela. +Kulitu kusankha, inde masankho. Dizilo Petulo Palibe, Polisi Palibe, Male Chauvinist Pigs ngakhalenso Ukafuna Dilu Fatsa akufuna kuonetsa kuti wamphamvu ndani. +Adatulukiranso Adona Hilida. Adanongoneza Kumbu kukhutu. +Iwe, masewera ayi. Ukapanda kutenga mipando, yako ntchito yatha zenizeni. Tapita ukatenge mipando, adatero Adona Hilida. +Adapitiriza: Kaya unama kuti wandilanda mpando; kaya unena kuti sunandilande, izo ndi zako. Koma utenge mpando. Pajatu Angoni a Chitumbuka ngati iwe ntchito zanu nzoopsa. +Nditero dona. Kodi uyu, Mzome, nambala yake muli nayo? Andimveke ufumu wanu basi. Kaya ndiutenga kaya sindiutenga, zonse adziwa ndi Ambuye, adatero Kumbu. +Komatu mukunamizana. Dikirani ndimuuze Koko Wakhuma zomwe mukukambirana, adatero Abiti Patuma. +Adaika foni yake pa loud kuti ndizimva. +Imeneyo isiye kaye. Iyo ndi nkhani yotentha. Nkhani yonona. Koma ndili kaye ku Ginnery Corner. Ndikufuna ntamudziwa Tadeyo, adatero Koko. +Nyaude: Tidadabwa ndi zochitika zake Akamaimba nyimbo ya Musalolere Mulungu Ephraim Zonda amaimba ndi mtima wonse polingalira kuti akulowa mbanja mwezi ukubwerawu ndipo Mulungu asalolere kuti adani alepheretse zimenezi. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Atupele ndi Ephraim kukonzekera kudzakhala thupi limodzi Ngati kumaloto, Ephraim akamakumbukira tsiku lomwe adaonana ndi Atupele Chikaya. Akuti sadadziwe kuti iwo akhoza kudzakumananso. +Ndidamuona koyamba Atupele ku tchalichi cha Zambezi ku Kawale komwe tinkakaimba. Panthawiyo sitidayankhulane koma mwachisomo cha Mulungu tidakumananso ku Chefa komwe tidakaimbanso, adatero Ephraim. +Mnyamatayu ndi wachiwiri kubadwa mbanja la ana asanu ndi awiri. Ali ndi luso lopeka nyimbo komanso ali ndi mawu anthetemya moti amaimba mukwaya ya Great Angels. Si zokhazo, amachitanso bizinesi yogula ndi kugulitsa katundu wochokera ku China kuphatikizapo galimoto. +Atupele ndi wachiwiri kubadwa mbanja la ana anayi ndipo amagwira ntchito ku Road Traffic ku Zomba. +Awiriwa adayamba kucheza muchaka cha 2009 pomwe adakumana ndipo patatha chaka akucheza chomwecho Ephraim adamufunsira Atupele ataona kuti ndi mkazi wabwino. +Atupele ndi mkazi amene ali ndi zomuyenereza zomwe mwamuna aliyense amafuna pa mkazi. Atu ndi mkazi wakhalidwe, woopa Mulungu, wanzeru komanso womvetsetsa, adatero Ephraim akunyadira bwezi lakelo. +Patatha zaka zisanu ndi chimodzi chikumaniraneni, awiriwa adaganiza zomanga ukwati kuti anthu atsimikize za chikondi chawo. +Ukwati wawo uliko pa 12 September chaka chino ndipo akadalitsira ku mpingo wa CCAP ku Area 23 mumzinda wa Lilongwe ndipo madyerero akakhala ku Capital Hotel. +Ephraim adanenetsa kuti chomwe chidzawalekanitse iwo ndi imfa basi. Iye adati nthawi yawathandiza kudziwana, zomwe iye akuti zidzawathandiza mbanja mwawo. +Mlandu wa Savala ukupendekeka Mlandu wa mayi wa zaka 33, Caroline Savala, yemwe khothi lidamupeza wolakwa pamlandu wakuba ndalama za boma zokwana K84 miliyoni ukuyenda mwapendapenda. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Savala yemwe amachita bizinesi ya zomangamanga adamupeza wolakwa ndipo akuyembekeza chigamulo cha khothi pa zachilango chake koma Lachisanu lapitali kudali ngati sewero ku bwalo la milandu pomwe womuimira pamlanduwo Ralph Kasambara adalephera kubwera kubwalolo. +Sadayankhe funso ngakhale limodzi: Savala (kumanzere) Kusabwera kwa Kasambara mmawa wa Lachisanulo kudakwiyitsa wogamula mlanduwo Fiona Mwale yemwe adaimitsa mlanduwo kuti upitirire 2 koloko masana. +Nkhaniyi ipitirira 2 koloko masana ano kuti woimirira mayi Savala abwere ndipo ngati sabwera tikamba nkhani popanda wowaimira,adatero Mwale. +Malingana ndi ndondomeko za ku bwalo la milandu, tsiku likakhazikitsidwa ndipo woimirira munthu pamlanduwo walephera kubwera pachifukwa chilichonse, amayenera kudziwitsa bwalo la milandulo nthawi yabwino kapena kutumiza okamuyimirira. +Mmawa wa Lachisanu, kalaliki wa kukhotilo adali kalikiliki kuyesetsa kulumikizana ndi Kasambara koma sizimatheke zomwe zidachititsa Mwale kuti asinthe nthawi ya mlandu. +Nthawi ya mlandu itafika 2 koloko masana, Kasambara sadaoneke kubwalo la milandulo ndipo mmalo mwake adatumiza womuimirira Tisilira Kaphamtengo, yemwe adapempha wogamulayo kuti mlanduwo awusuntheso poti iye samautsatira bwinobwino. +Ine ndiwongoimirira a Kasambala omwe sakumva bwino mthupi koma poti nkhaniyi sindikuyitsata bwinobwino ndimati ndipemphe kuti isinthudwe ndipo idzakambidwe tsiku lina, adapempha Kaphamtengo. +Mwale adakana kumva pempholi ponena kuti zomwe adauza khothi Kaphamtengo zokhudza kusamva bwino mthupi kwa Kasambala amayenera kuuza bwalolo nthawi yabwino ndipo adati mlanduwo upitirirebe. +Mwale atanena izi, Kaphamtengo adapemphanso kuti alole kuti Savala asayankhe funso lililonse limene afunsidwe poopa kupotoza nkhani ndipo pempholi lidaloledwa. +Savala adafunsidwa mafunso 10 koma sadayankhepo ngakhale limodzi mpaka mlanduwo udayimitsidwa. +Savala adapezeka wolakwa pa 18 July 2015 wogamula yemwe adalinso Mwale atapeza umboni wakuti mayiyu amalandira ndalama zosagwirira ntchito kuchoka ku unduna wa zokopa alendo. +Savala,yemwe samagwira ntchito mboma nthawi yomwe amaganiziridwa kuti amalandira ndalamazo, adauza bwalo la milandu muumboni wake kuti iye adachita kukokeredwa mu kangaude wachinyengowu ndi mkulu wina yemwe amagwira ntchito ku unduna wazokopa alendo Leonard Kalonga komanso mnzake wa ku ubwana Florence Chatuwa omwenso amayimbidwa mlandu omwewo. +Sakumvanabe pa nkhani za ufumu Pali kusamvanabe pakati pa unduna wa maboma aangono ndi mafumu a mmizinda amene boma, kudzera mu undunawu, lidawalembera kalata yowadziwitsa kuti asagwirenso ntchito yawo mmizindayi. +Kusamvanaku kwadza pamene zamveka kuti boma tsopano lasintha ganizo popempha mafumuwa kuti ayambirenso kugwira ntchito yawo. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Senior Chief Kapeni, yemwe ali nawo mkomiti yomwe mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adakhazikitsa kuti ifufuze za kuchotsedwa kwa mafumu a mmizinda, watsimikiza za nkhaniyi. +Kapeni adauza Tamvani kuti Loweruka lapitali iye pamodzi ndi mafumu ena T/A Ngolongoliwa wa mboma la Thyolo, Senior Chief Chikumbu wa mboma la Mulanje ndi T/A Malemia wa ku Zomba adasonkhanitsa mafumu okhudzidwawo mumzinda wa Blantyre kuwauza kuti ayambirenso kugwira ntchito yawo. +Koma izi zikusemphana ndi zomwe Tracizio Gowelo, nduna ya maboma aangono, wanena pankhaniyi. +Sindikudziwapo kanthu kuti mafumuwa auzidwa kuti ayambe kugwira ntchito [mumizinda], adatero Gowelo. Ndikudziwadi kuti pali komiti yomva maganizo ndipo a Kapeniwo ali mkomitiyo. Chomwe ndikudziwa nchakuti zokambirana pankhaniyi zidakali mkati. +Nanga zoti ayambirenso kugwira ntchito mmizinda mafumuwa akuzitenga kuti? Ngolongoliwa akuti ganizo loti ayambirenso kugwira ntchito labwera pambuyo pa zokambirana zomwe adali nazo ndi a unduna wa maboma aangono. +Mzokambiranazo mudali mlembi wa undunawu [Chris Kangombe] komanso a Makonokaya [Lawrence] ndi mafumu ena amene tili mkomitiyi. Tidagwirizana kuti mafumuwa ayambirenso kugwira ntchito yawo. +Panopa mafumu a mumzinda wa Blantyre ayamba kale kugwira ntchito ndipo kwatsala ndi ku Luchenza komwe timafuna tipite sabata ino koma zavuta chifukwa cha maliro, adatero Ngolongoliwa. +Tidalephera kulankhulana ndi Makonokaya chifukwa adatuluka mdziko muno pamene Kangombe adati tilankhule ndi mneneri wa undunawu, Muhlabase Mughogho. +Naye Mughogho adati woyenera kulankhulapo ndi wamkulu wa mafumuwa [Director of Chiefs] Makonokaya. +Monga Kapeni akunenera, zokambirana zawo ndi boma ndizo zidabala mfundo yoti mafumuwa apepesedwe powavula ufumuwo ndiponso kuwadziwitsa kuti ayambirenso kugwira ntchito yawo. +Tidaitanidwa ndi mafumu ena a zigawo za Kumpoto, Pakati, Kummwera komanso Kummawa kuti tikambirane za kuchotsedwa kwa mafumu a mmizinda. A ku OPC [Office of the President and Cabinet] ndi omwe adatiitana. +Padalibe zokambirana zenizeni koma iwowo adatiuza kuti a Pulezidenti sadanene kuti mafumu asiye kugwira ntchito [mmizinda] ndipo adatiuza kuti tiyambe kuyenda mmizindayi kuwauza mafumu amene adachotsedwawo kuti ayambirenso kugwira ntchito yawo, adatero Kapeni. +Koma mneneri wa Pulezidenti, Gerald Viola, adati nkhaniyi ikuyendetsedwa ndi nduna ya maboma aangono kotero tifunse Gowelo. +Titamuuza kuti Gowelo sakudziwapo kanthu kuti mafumu ayamba kugwira ntchito mmizinda, Viola adati: Zitheka bwanji kuti iwowo asadziwe poti nkhaniyi ikukhudza unduna wawo? Zitha kutheka kuti iwowo sali mkomiti yomwe ikumva maganizoyi, koma sizingatheke kuti asadziwe chomwe chikuchitika. Dikirani ndilankhulane nawo kaye, adatero Viola. +Koma Kapeni wanenetsa kuti mafumuwo awauza kuti kalata yomwe idalembedwa ndi undunawu yasiya kugwira ntchito ndipo auzidwa zoyambiranso ntchito. +Kalatayo idakambapo za gawo 3 (5) la malamulo okhudza ufumu (Chiefs Act) lomwe likuletsa mafumu a mmizinda monga Luchenza, Lilongwe, Mzuzu, Zomba komanso Blantyre kugwira ntchito yawo, komanso idanenetsa kuti mafumuwa achotsedwa pamndandanda wolandira mswahara. +Kalatayo, yomwe idasainidwa ndi Makonokaya, idati yakhala ikuchenjeza mafumuwa kuti asiye kugwira ntchito koma sadamvere. +Mafumu ena mumzinda wa Blantyre monga gulupu Misesa, ndi nyakwawa Makata atsimikiza kuti ayamba kale kugwira ntchito yawo. +Wa zaka 18 akaseweza zaka 18 Bwalo lamilandu mumzinda wa Mzuzu lagamula Mulolo Nkhata wa zaka 18 kukakhala kundende zaka 18 atamupeza wolakwa pamlandu wogonana ndi mwana wa zaka 6. +Zidamveka mbwalolo kuti mnyamatayo ankagwira maganyu kunyumba kwa makolo a mwana ochitidwa chipongweyo ndipo kaamba ka kubwerabwera kwake pakhomopo adayamba kudziwana ndi yo. +Nkhata ndi wochokera mmudzi mwa Chikwina T/A Nyalubanga mboma la Nkhata Bay. +Mneneri wa polisi mumzinda wa Mzuzu Patrick Saulosi adati Nkhata adavomera kulakwa kwake pamlanduwo. +Iye adati woimira boma pamlanduwu, sub-inspector Lyson Kachikondo, adapempha bwalo lamilandu kuti chigamulo chikhale chokhwima kaamba kakuti mlanduwu ndiwaukulu komanso zomwe wamudutsitsa mwanayo ndi chinthu chomwe sangadzaiwale moyo wake onse. +Ogamula mlanduwu, Tedious Masoamphambe adavomereza zomwe adanena Kachikondo ndipo adati chigamulo chachikulu chithandiza kuchepetsa kuchuluka kwa milandu ya ntunduwu, adatero Saulosi. +Izi zili choncho bambo wa zaka 47, Wilson Nyirenda, wa mboma la Nkhata Bay wagamulidwa kukhala ku ndende zaka 14 atagonana ndi mwana wa zaka 12. +Mneneri wa polisi wa mboma la Nkhata Bay Ignatius Esau adati mwezi wa August, Nyirenda yemwe ndi wochokera mmudzi mwa Chikalanda T/A Chikulamayembe ku Rumphi adamuitanira mwanayo mu nyumba mwake momwe adamugwiririra. +Mwanayo adatuluka mnyumbamo akulira zomwe zidachititsa anthu kuti amufunse zomwe zamuchitikira ndipo mwanayo adaulula, adatero Esau. +Iye adati Nyirenda adakana mulanduwo koma adapezeka wolakwa anthu anayi atachitira umboni za nkhaniyi. +Iye adati anthu ankamunamizira chifukwa amachita naye nsanje poti siochokera mmudzimo. Adauzanso bwalolo kuti adali ndi matenda a chinzonono ndipo adauza makolo a mwanayo kuti apite naye kuchipatala. Adapitiriza kuti adakhala nthawi yaitali asadagonane ndi mkazi ndipo ngati adagwiririradi mwanayo ndiye kuti adampatsa mimba, adatero Esau. +Iye adati ogamula mlanduwu, Billy Ngosi, adati milandu yogwiririra ikukula ndipo olakwa akuyenera kupatsidwa chigamulo chonkhwima kuti chikhale chiletso kwa ena. +Katundu wakwera udyo, atero anthu Amalawi akonzekere kulira chifukwa cha kukwera udyo kwa mitengo ya zakudya ndi katundu wina komwe kwachitika kuyambira mwezi wa June chaka chino, latero bungwe la Centre for Social Concern, lomwe limaona momwe moyo wa anthu ukuyendera pankhani za chuma. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Bungweli lati kafukufuku wawo waonetsa kuti mmaboma a Karonga, Mangochi, Mzuzu, Lilongwe, Zomba ndi Blantyre, zakudya zakwera mtengo zomwe zivulaze Amalawi. Nawo anthu mmidzi akuti ali pamoto ndi kukwera mtengo ka zakudya. +Zakudyazi ndi monga nyemba, mpunga, usipa, bread, sugar, mafuta ophikira, chimanga, chinangwa ndi zina zomwe munthu amayenera agwiritse ntchito pa tsiku. Bungweli lati ichi ndi chisonyezo kuti miyezi tikulowayi zinthu zinyanya kuwawa chifukwa chakusokonekera kwa chuma. +Kafukufuku amene bungweli lachita mmiyezi ya June ndi July waonetsa kuti banja la anthu 6 tsopano likuyenera kukhala ndi K126 457 kuchoka pa K118 663 yongogwiritsira ntchito mwezi umodzi. +Mmiyezi yomweyi chaka chatha, zakudya zidatsika mtengo ndi pafupifupi K2 pa K100 iliyonse. Ichi ndi chisonyezo kuti tikuloweraku anthu avutika kuti akwanitse kudya, mbali imodzi ya kafukufukuyo yatero. +Izi zikusiyana ndi zomwe nduna ya zachuma Goodall Gondwe idauza mtundu wa Amalawi mu February chaka chino pamene idati kuyambira miyezi ya July ndi September zinthu zidzayamba kuyenda bwino. +Kusefukira kwa madzi ndiko kwatisokoneza kuti chuma chisayende bwino koma tikuyembekeza kuti pofika gawo lachitatu la chaka [July mpaka September] 2015 zinthu ziyamba kuyenda bwino, adatero Gondwe pouza The Nation. +Bungweli lati mmwezi wa July, mtengo wa nyemba udakwera ndi K15 pa K100 iliyonse. +Kumbali ya chimanga ndiye chidakwera ndi K6 pa K100 iliyonse mu June ndipo chakweranso mu July. Thumba la makilogalamu K50 likugulitsidwa K6 389 mmizinda ikuluikulu. +Ku Blantyre ndi Mangochi, mtengowu wafika pa K8 000 ndi K7 500 motsatizana. Zinthu zina monga sugar ndi nyama zakwera ndi pafupifupi K4 pa K100 iliyonse mu June ndipo mitengoyi yakweranso mu July, watero kafukufukuyu. +Izi zikutsatiranso zomwe komiti yomwe imaona momwe chakudya chilili ya Malawi la Vulnerability Assessment Committee (MVAC) idatulutsa kuti pafupifupi anthu 3 miliyoni mdziko muno akhudzidwa ndi njala ndipo afunika thandizo kwa miyezi isanu ndi umodzi. +Mkulu wa bungwe loona ufulu wa ogula la Consumers Association of Malawi (Cama) John Kapito wati nthawi yakwana kuti mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika abwere poyera ndi kufotokozera Amalawi zomwe achite pofuna kupulumutsa anthu kunganjo yowawitsayi. +Vuto ndi mtsogoleri wathu chifukwa sakulankhulapo chilichonse. +Taonani momwe ndalama yathu ikuchitira, mudamuonapo [pulezidentiyu] akuwauza Amalawi chomwe achite? Akuyenera kupereka chikhulupiriro kwa Amalawi momwe titulukire mmavutowa. Akuchita ngati zinthu zikuyenda bwino pamene anthu akuvutika, adatero Kapito. +Mneneri wa Mutharika Gerald Viola adati atiyimbira kuti afotokozepo mbali ya mtsogoleri wa dziko Peter Mutharika, koma pofika nthawi yomwe timasindikiza nkhaniyi iye adali asadatipatse mbali yake. +T/A Kanduku wa mboma la Mwanza akuti mbomalo mudali chilala choopsa chomwe chachititsa kuti anthu asamadye katatu patsiku. +Kumudzi kuno ndi ochepa amene ungawapeze akudya mmawa, masana ndi madzulo. Ambiri akungodya madzulo okha. Chimanga chakwera mtengo. Ndowa tikugula K 3 000 pamene thumba ndi K9 000, adatero Kanduku. +Clara Nyandula wa mboma la Balaka akuti kumeneko thumba la chimanga lafika pa K8 500 ndipo anthu ambiri akumagula chimanga cha mbigili pamtengo wa K1 000. +Zikatere, kudya mwakasinthasintha nkomwe kungathandize kuti anthu ayambe kudalira zakudya zina monga chinangwa, nthochi ndi mpunga. +Dz Young Soccer, Mighty adutsa Chikho cha Standard Bank chayamba ndi moto pamene matimu a asirikali a Kamuzu Barracks ndi Mafco FC aona msana wa njira atakwapulidwa ndi Dedza Young Soccer FC komanso Be Forward Wanderers kudzera mmapenote. +Chikho cha K10 miliyonichi chidayamba modabwitsa Lachitatu pamene timu ya Kamuzu Barracks idaona mdima pa Civo Stadium itachitidwa chiwembu ndi Dedza Young Soccer kudzera mmapenote. Masewerowo adathera 2-2 ndipo nthawi ya mapenote Young Soccer idalimba chifu pokakamizabe asirikaliwa kuti atuluke mchikhochi. 10 kwa 9 ndi momwe mapenotewo adathera, kukomera anyamata a ku Dedza. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Lachinayi udalipoliponso pabwaloli Wanderers kulimbana ndi asirikali a Mafco. +Masewerowanso adatheranso mmapenote atalepherana duu kwa duu ndipo Wanderers idapuntha Mafco 4-3 mmapenotewo. +Mafco idali ndi mwawi wambiri moti ikadatha kuchinya zigoli mphindi 90 koma zonse zidangothera hiii! Iyitu idali ndime yachipulula ndipo matimu amene achita bwinowa alowa mndime ya makotafainolo. Apa ndiye kuti Dedza iphana ndi Civo mndimeyi pamene Wanderers ikumana ndi Red Lions. +Mmakotafainolo ena, timu yomwe ikuteteza chikhochi, Silver Strikers, ikwapulana ndi Blue Eagles pamene Moyale Barracks ikumana ndi Big Bullets. +Kochi wa Wanderers Elia Kananji adati ali ndi chiyembekezo kuti timu yake ichita zakupsa mchikhochi. +Adali masewero ovuta koma Mulungu adali mbali yathu. Tikukhulupirira kuti Mulungu yemweyo akhala nafe mumpikisanowu mpaka kumapeto, adatero Kananji. +Naye Pofera Jegwe, kochi wa Dedza Young Soccer, adati kupambana kwawo ndi chithokozo kwa masapota awo. +Mukudziwa kuti tidachita kuvoteredwa kuti tisewere mchikhochi, ndiye kupambanaku ndi njira imodzi yothokoza amene adativoterawo, adatero Jegwe. +Bungwe la FAM lomwe likuyendetsa mpikisanowu litulutsa masiku amene makotafainolowa aseweredwe. +Anatchezera Ndimamukonda Agogo, Ndinali pachibwenzi ndi mkazi wina ndipo zaka ziwiri zatha pomwe tinasiyana. Pano ali ndi mwana yemwe wabereka mwezi watha ndiye akumabwera kwa ine nkumati tibwererane. Kodi pamenepa ndithani, agogo? Mkaziyo kunena zoona ndimamukonda, koma pano ndinalimba mtima. Nditani? Ine Amfumu, Zingwangwa Amfumu, Nkhani yanu ndi yovuta kuitsata bwinobwino chifukwa simukumasula kuti vuto lanu ndi chiyani jwenikweni. Poyamba mwanena kuti mkaziyo munasiyana naye zaka ziwiri zapitazo, munasiyana chifukwa chiyani? Mwati pano mkaziyo akuti mubwererane ndipo inu nomwe mukuti kunena zoona ndimamukonda. Komanso inu nomwenso mukuti pano munalimba mtima, mukutanthauzanji? Mwatinso mkaziyo ali ndi mwana wa mwezi umodzi, nchachidziwikire kuti mwanayo si wanu-poti mwanena nokha kuti chibwenzi chanu chidatha zaka ziwiri zapitazo. Apatu, kunena zoona Amfumu, mayankho muli nawo ndinu. Ngati mkaziyo mukuti mumamukonda, chovuta nchiyani kuti mubwererane? Koma mukuti mwalimba mtima, kulimba mtima kotani? Nchifukwa chake ndikuti zonse zili ndi inu kuti mubwererane kapena ayi poti zifukwa zake zomwe mudalekanirana mukuzidziwa ndinu. Mwakula mwatha, Amfumu. +Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Akufunabe wakale? Agogo, Ndili ndi mkazi yemwe ndabereka naye ana atatu koma nthawi zambiri wakhala akumafunabe chibwenzi chake chakale chomwe chidamusiya. Ndakhala ndikupeza ma SMS olemba I LOVE U MPAKA KALE pafoni. Ndikamufunsa amathamangira kupepesa. Kodi andithandiza ameneyu? Ndinganene kuti ndidapezadi mkazi kapena ndiyangane wina? Chonde ndithandizeni. +Ine Che Mwenye Che Mwenye, Pa Chichewa pali mawu oti madzi saiwala khwawa. Mawuwa akutikumbutsa kuti pali anthu ena amene akakhala pachibwenzi, ngakhale chibwenzicho chitatha akakumana amakumbutsa chikale; amathanso kumachitirana nsanje, chonsecho chibwenzi adathetsa pakati pawo. Mchitidwe kapena khalidwe lotere silofunika anthu mukakhala mbanja chifukwa tanthauzo lake nloti wina akuzembera mnzake wabanja pokhala ndi chibwenzi kapena zibwenzi zamseri. Wina akangozindikira kuti mnzangayu akundiyenda njomba, ukwati nthawi zambiri sulimba. +Tsono apa kunena mwachindunji, mkazi wanuyo alibe chilungamo chifukwa sangamalembe kapena kulandira ma SMS achikondi kwa wina inu mulipo. Malamulo a mbanja amakana zimenezi, chifukwatu munthu wotere sunga mukhulupirire. Banja lagona pachikondi ndi chikhulupiriro kwa wina ndi mnzake. +Komanso inu, abambo, muli ndi vuto. Akazi anu akachokapo basi muli pafoni gwi! kuyangana kuti waimba ndani kapena kumayangana ma SMS. Si bwino kumatero chifukwa zimaonetseratu kuti mbanja mwanu simukhulupirirana.Chomwe mungachite apa ndi kukhala pansi ndi akazi anu kuwafotokozera bwino lomwe za kuipa komagonekerana khosi ndi bwenzi lawo lakale pomwe tsopano ali ndi inu. Ngati akupiririzabe mchitidwe wotere, muli ndi zifukwa zokwanira zothetsera banja chifukwa mkazi sakhala ndi mitala. Pajatu amati mapanga awiri avumbwitsa. +Utsi ku Nam pamene ma Queens anyamuka Utsi ukufukabe ku bungwe loyendetsa masewero a ntchemberembaye la Netball Association of Malawi (NAM) kaamba kosemphana zochita pakati pa mphunzitsi wa timuyi Peace Chawinga-Kalua ndi bungweli. +Timu ya ntchemberembaye yomwe imangodziwika kuti Malawi Queens idanyamuka mdziko muno Lachitatu msabatayi ulendo ku Sydney mdziko la Australia komwe ikukapikisananawo mchikho chapadziko lonse. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Kugwebana kudayambika pamene zidadziwika kuti NAM idatumiza kale maina a atsikana amene apita ku Australia mosadziwitsa Kalua. +Malinga ndi Kalua, NAM idatumiza maina a osewerawo pamene iye asadawaitane kukampu kuti akachite zokonzekera. +Ineyo ndi amene ndimayenera ndisankhe osewera amene achita bwino kukampuko. Koma zomwe zachitika nkuti NAM yasankha kale osewera ine ndisakudziwa. Nditatulutsa mndandanda wa osewera anga amene ndikuwafuna, iwo akana osewera ena amene ndawapatsa ndipo aika amene akuwafuna, adatero Kalua. +Queens captured on departure at Chileka Airport in Blantyre. +Koma pamene amanyamuka pa bwalo la ndege la Chileka Lachitatu, nkhope za akuluakulu a NAM ndi mphunzitsiyu zimaoneka kuti sizikumvana zochita. +Chitsanzo, titamufunsa mphunzitsiyu zomwe akonzekera kukabweretsa kuchokera ku mpikisanowo, iye adati, funsani amene akonzekera kukabweretsa zotsatira zomwe mukufunsazo. Ine sindingayankhe zimenezo, adatero mphunzitsiyu uko akusonya a NAM kuti atifotokozere. +Koma titamufunsa pulezidenti wa NAM Rose Chinunda, iye adati sakuonapo vuto chifukwa ganizolo lidachitika atakambirana ndi wachiwiri kwa Kalua yemwe ndi Mary Waya komanso Griffin Saenda yemwe ndi wothandizira aphunzitsiwa kagwiridwe ka ntchito yawo. +Tidafunsa anthu amenewa koma mphunzitsi yekha ndiye sitidamufunse. Ganizo lochotsa wosewera wina ndikubwereretsapo wina lidabwera titamva kwa awiriwa, ndiye palibe vuto komanso dziwani kuti majority rules [timamvera anthu ambiri popanga ganizo] adatero Chinunda. +Komabe izi zakhumudwitsa kampani ya Airtel Malawi yomwe imathandiza atsikanawa. Mneneri wa kampaniyi Edith Tsilizani adapempha mbalizi kuti zikambirane ndikuthetsa kusamvanaku. +Ndizodandaulitsa kuti pali chimkulirano chotere, koma ife tikupempha kuti akambirane ngati akufuna kuti tikabwere ndi zotsatira zabwino kuchokera ku ulendowo, adatero Tsilizani yemwe kampani yake idapereka K7 miliyoni pa ulendowu. +Kalua amafuna atenge Ellen Chiboko wa Tigresses koma mmalo mwake NAM idachotsa dzina lake ndikuikapo Jean Chimaliro zomwe zadabwitsa. +Uwu ndi mndandanda wa osewera amene anyamuka ulendo ku Sydney; Mwawi Kumwenda, Joyce Mvula, Towera Vinkhumbo, Carol Ngwira, Sindi Simtowe, Takondwa Lwazi, Chimaliro, Grace Mhango, Lauren Ngwira, Thandi Galeta, Bridget Kumwenda ndi Martha Dambo. +Atsikanawa adatsimikiza kuti ngakhale pali kusamvana komabe ulendo wa ku Sydney akukamenya nkhondo. +Mwambo wogwetsa simba Sukulu zatsekera ndipo zikatere mmaboma ambiri makolo ali kalikiriki kukonzekera kuti ana awo apite kusimba kukavinidwa. Kumenekotu kumakhala uphungu kuti anawa adziwe khalidwe komanso momwe zina za mbanja zimakhalira. Zambiri zakhala zikukambidwa zokhudza unamwaliwu koma sabata ino BOBBY KABANGO akutibweretsera mwambo womwe umachitika pamene anamwali akutulutsidwa kusimba pachinamwali cha jando. Kodi zimakhala bwanji? Tidziwane Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Ndine Evason Chalamanda, wamkulu wa simba muno mmudzi mwa Malika, kwa T/A Mpama mboma la Chiradzulu. Ngati mukufuna kudziwa chilichonse cha simba, ine ndiye mwini wake. +Timamva kuti kumakhala mwambo patsiku lomwe mukusasula simba, kodi ndi zoona? Zimenezo ndi zoonadi, chinamwali ndi mwambo ndiye pamene mwamaliza kulanga anamwali, mumayeneranso kuti mutsate mwambo womwewo ngati mukusasula simba. Ndigwirizane nanu kutidi pamakhala mwambo. +Umakhala mwambo wanji? Mwambo wosangalala basi, kuti tamaliza chinamwali. Tikawasunga anamwaliwa kwa sabata zitatu, ndiye tsiku lomwe tikuwatulutsa timayenera kukhala ndi mwambo basi. +Mwambowo umachitikira kuti? Malo alionse oyandikana ndi simbalo koma usachitikire kunyumba. Mumangotuluka kusimbako ndi kukhala chapafupi ndi simbalo. Mwambowu suchitikira kusimba chifukwa kumakhalabe anamwali. Dziwani kuti mwambowu ukamayambika anamwali amakhala asanatulutsidwe ndipo amadzakupezani mwambowo uli mkati. Komanso dziwani kuti amayi ndi anthu amene sadavinidwe sayenera kufika kusimbako nchifukwa mwambowo suchitikira kumeneko. +Bwanji osangopangira kusimba komweko? Pamene tikusasula simba, timafuna tisangalale ndi anzathu. Makolo, achibale komanso anzathu kuchokera midzi yosiyanasiyana amabwera. Poti anthuwa saloledwa kufika kusimba, nchifukwa chake timachoka kusimbako kuti tikumane malo abwino. Anthuwa amakhala akufupa anamwaliwa pamene atuluka kusimbako. +Kodi kumakhala zochitika zotani patsikuli? Aliyense amachita monga akufunira koma kunoko timakhala ndi mwambo wosangalala ndi magule, timakhala ndi azungu komanso chinyama zomwe zimasangalatsa anthu amene abwera kudzaonerera mwambowo. +Azungu? Eya, kapena kunena kuti anthu amene khungu lawo ndi loyera. +Amachokera kuti? Amachokera kusimba komweko! Ndi a mdziko lomwe lino? Kapena mumachita kupangatu inu Ndi anthu amene amakhala kusimbako koma amakhala kuti adavinidwa kale. Awa si anamwali chifukwa anamwali amatuluka usiku basi, pamenenso kumakhala mwambo wina. +Kodi ndi azungudi? Kapena mundipusitsatu Amenewa si azungu enieni, timachita kupanga kusimba komweko. Timatenga dothi nkuliviika mmadzi. Likafewa timawauza kuti ayambe kudzola thupi lonse ndipo likauma munthuyo amafanana ndi mzungudi. +Amaoneka bwanji? Khungu ngati mzungu, koma mavalidwe ndiye amavala zosiyasiyana chifukwa ena amavala nsalu, ena dilesi ndiye amaoneka ngati atsikana koma onse ndi anyamata. +Ndiye mwati kumabweranso chinyama? Eya ndipo chimakhala chofanana ndi mbalame. Dzina lake timachitcha chimwanambera. Ntchito yake nkuopseza ana kuti adziwe za kuopsa kwa samba. Paja ndanena kuti kumabweranso ana koma sikuti chimawamenya. +Mumachitanso kupanga? Eya, timachipanga ndi mitengo, kunjako timachikutira ndi bulangete kapena nsalu. Mkatimo mumakhala anthu awiri kapena mmodzi kuti azichiyendetsa. +Msewu wa Rumphi-Nyika udzatheka? Mkonzi, Ndafuna ndipereke chidandaulo kuboma lathu kudzera mnyuzi yathuyi komanso kwa phungu wa dera lathu la Rumphi West Hon Jacquilline Kouwenhoven kuti atiganizire za msewu wa Nyika womwe wakhala zaka zambiri osauganizira chonsecho ndi msewu wofunika kwambiri pachitukuko cha dziko lino, maka kumbali yokopa alendo. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Tsiku ndi tsiku alendo ochokera kumaiko akunja komanso ena a mdziko mwathu mommuno amadzera msewuwu kuchoka pa Rumphi boma kupita ku Nyika National Park kukacheza ndi kukaona zinyama. Kunena zoona, Nyika ndi malo okongola kwambiri ndipo amene adapitako amafananiza malowa ndi ku Mangalande. Koma ndikukaika ngati akabwerera kwawo amakhalanso ndi chilakolako choti adzabwererenso tsiku lina kumalowa chifukwa msewu wake ndi wosautsa kwambiri. +Msewu wopita kumalo okopa alendowa ndi umenewu Nthawi yachilimwe ngati ino si mabamphu ndi fumbi lake kuchokera paboma kukafika ku Nyika moti alendo amakfika ali mbuu kutuwa ngati nyau komanso atatopa kotheratu. Nthawi yadzinja ndiyenso kumakhala ntchito chifukwa si matope ake moti ena amangobwerera paboma osakafika ku Nyikako. +Komanso msewu wa Nyikawu ndiye wachidule kwa anzathu omwe amakhala ku Nthalire ndi Wenya mboma la Chitipa. Utakhala kuti waikidwa phula ndiye kuti nawonso awomboledwa kumbali ya maendedwe. Sakazunguliranso ku Karonga mpaka kukafika paboma la Chitipa kenaka nkumalumikiza kukafika kwawo. +Ife alimi timavutika kwambiri kupita ndi katundu wathu kumisika chifukwa cha kuonongeka kwa msewuwu komanso timalipira ndalama zambiri tikakwera galimoto. +Chonde, nafe ndife Amalawi, tithandizeni. +Kudali kumapemphero Mawu a Mulungu amati: Kodi simudziwa kuti iwo akutumikira za mkachisi amadya za mkachisi Mawu a Mulunguwa adakwaniritsidwa pomwe Rose Cross adakumana koyamba nkudyererana maso ndi Ephod Mahorya kumapemphero. +Panthawiyo Rose ankapembedza kumpingo wa Living Word ndipo Ephod adali wa mpingo wa Church of Nazarene. Ngakhale ankapemphera kumipingo yosiyana, awiriwa ankakumana kumapemphero mkati mwa sabata. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Tsopano ndi thupi limodzi: Rose ndi Ephod patsiku la ukwati wawo Rose ndi woyamba kubadwa mbanja la ana atatu ndipo akugwira ntchito ku unduna wa zofalitsa nkhani komwe ndi mtolankhani wa Malawi News Agency (Mana), pomwe Ephod ndi wachitatu kubadwa mbanja la ana asanu ndi awiri ndipo amagwira ntchito ngati msungichuma kubungwe la Compassionate Stewards. +Rose adati iwo atakumana adayamba kucheza ngati munthu ndi mnzake koma kumapeto kwa chaka cha 2013 ndi pomwe Ephod adamumasulira Rose za chikondi chomwe chinkasefukira mumtima mwake iye ndipo Rose naye adaulula za mumtima mwake. Uku kudali kuyamba kwa chikondi chawo. +Awiriwa adamanga ukwati woyera mumzinda wa Mzuzu pa 4 July chaka chino ndipo mwambo womanga banjalo udachitikira ku Church of Nazarene kenaka madyerero adachitikira ku Victory Temple komwe anthu adachita perekaniperekani wamphamvu nkudyerera ndi kumwerera mwachimwemwe. +Ephod amachokera mmudzi mwa Mumbo, mfumu yaikulu Jenala mboma la Phalombe, pomwe Rose ndi wa mmudzi mwa Yohane Jere, Inkosi Mtwalo, mboma la Mzimba. +Ndimamukonda Ephod, makamaka chifukwa cha mtima wake wokonda Mulungu, komanso ndi munthu wachikondi kwambiri ndipo satopa kuthandiza anthu ovutika, adatero Rose monyadira. +Ephod naye sadabise mawu. Adati amamukonda Rose kaamba ka khalidwe lake labwino ndi mtima wake wansangala komanso wachikondi. +Amukwidzinga Pachinkhoswe Amati mbuzi ikakondwa amalonda ali pafupi. Nzoonadi, Ili lidali tsiku lachisangalalo ndipo kudali kuvina, amayi nthungululu zili pakamwa. Anthu adabwera mwaunyinji kudzachitira umboni pachinkhoswe cha awiriro, koma mapeto ake chisangalalocho chidasanduka chisoni. +Wojambula wathu kufanizira momwe zidalili patsikulo Inde, lichero lidali lili mmanja, anthu akuzungulira kuti afupe limodzilimodzi uko akuvina. Koma mwadzidzidzi ena amene amabwera ngati akufuna adzaponye adali apolisi amene adafikira kumuveka unyolo mmalo momufupa. +Ngati kutulo izi ndi zomwe zidachitika pa 31 July mdera lotchedwa Chilobwe, mmudzi mwa Kaumphawi, T/A Nsamala ku Balaka, komwe apolisi adanjata bambo wa zaka 27 patsiku lomwe ankachita chinkhoswe chake. +Mneneri wa polisi mboma la Balaka, Joseph Sauka, watsimikiza za kunjatidwa kwa Mabvuto Michael, wa mmudzi mwa Njalanja, kwa T/A Nsamala mbomalo pomuganizira kuti adaba nkhumba. +Sauka adauza Msangulutso Lachiwiri kuti Michael akuganiziridwa kuti adapalamula mlanduwu mu April chaka chino ndipo apolisi akhala akumusaka kwanthawi yaitali koma samamupeza. +Patsikuli tidatsinidwa khutu kuti amuona woganiziridwayu ku Chilobwe komwe akuchititsa chinkhoswe. Wotitsina khutuyo adayamba wapita kaye kumaloko ndipo atatsimikiza kuti ndi yemweyodi, adadzauza apolisi ndipo tidathamangira kumaloko kukamugwira. +Sitinafune kuti timudikire amalize zachinkhoswezo chifukwa timaopa kuti mwina angatithawenso ndipo tidamukwidzinga nawo unyolo lichero lili mmanja uko anthu akufupa. Zonsezo zidathera panjira chifukwa chomangidwa kwake, adatero Sauka. +Iye adati anthu amene adatchena zachinkhoswe limodzi ndi namwali yemwe bamboyu amachititsa naye chinkhoswe adangogwira chala pakamwa, osakhulupirira kuti chikuchitika nchiyani. +Lachiwiri Michael akuti adakaonekera kubwalo lamilandu mbomalo komwe adaukana mlandu woba nkhumba womwe ndi wotsutsana ndi gawo 278 la malamulo ndi zilango zake. +Zakudya za ziweto zasowa Mboma la Nsanje, ziweto monga ngombe, nkhosa ndi mbuzi zili pamoto chifukwa cha kusowa kwa chakudya. +Kwauma, ndipo tchire anthu atentha. Nthawi ngati imeneyi zaka zonse, ziweto akuti zimadalira kumtsinje wa Ruo komwe zimakadya bango, nsenjere ndi udzu wauwisi. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Koma chaka chino chifukwa cha madzi osefukira, Ruo wabweretsa mchenga wambiri zomwe zachititsa kuti bango ndi udzu wauwisi ukwiririke. Mulibemo msipu ulionse. +Malinga ndi gulupu Manyowa, ziwetozi zikudalira makoko a chimanga, nthochi kapena zikonyo mwinanso mango. +Ziweto zambiri zikumasonkhana pansi pa mitengo ya mango kuti anthu akamathyola zidyeko. Chifukwa cha kusowa chakudya, ziweto zambiri zaonda, adatero Manyowa. +Koma alangizi amalangiza kuti zikatere alimi amayenera kuti azikhaliratu atapanga zakudya za ngombe ndi mbuzi kuti azizipatsa nthawi ngati ino. +Manyowa akuti mmudzi mwake palibe munthu amene adapanga zakudyazo chifukwa cha mavuto a madzi amene adakumana nawo. +Palibe amene adapanga zakudya za ziweto. Kodi mmene zidalili kuno ungamupeze munthu akupanga zakudya za ziweto? Mlimi aliyense adali ndi chiyembekezo kuti ziweto zizikadyera kumadzi monga zikhalira nthawi zonse osadziwa kuti kukhala mchenga wotere, adaonjeza. +Mneneri mu unduna wa zamalimidwe, Hamilton Chimala, akuti alimi akuyenera kumakhala okonzeka ngati akufuna ziweto zawo zipulumuke nyengo ngati ino. +Boma litemera ziweto 10 000 Pofuna kuthana ndi mliri wa matenda a zilonda za m mapazi ndi mmkamwa a ngombe omwe agwa mboma la Chikwawa, boma lakonza zopereka katemera ku ziweto zoposa 10 000 mchigwa cha Shire posachedwapa. +Mlembi wa unduna wa zamalimidwe, ulimi wamthirira ndi chitukuko cha madzi, Erica Maganga, watsimikizira Uchikumbe kuti boma laitanitsa kale mankhwala a katemerayu kuchoka kudziko la Botswana. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Pakalipano mankhwala ali mnjira ndipo akhala akufika tsiku lina lililonse kuti ntchito yopereka katemera iyambike, adatero Maganga Lolemba. +Iye adati boma lachita machawi poitanitsa katemerayu pofuna kuti matendawa asafalikire mmadera ena komanso pofuna kuteteza ntchito zina za ulimi monga ulimi wa mkaka. +Boma lidakhazikitsa chiletso cha malonda a nyama ndi kutulutsa kapena kulowetsa ziweto mboma la Chikwawa zitatsimikizika kuti mbomali mudagwa mliri wa matendawa omwe pachizungu amati Foot and Mouth Disease. +Unduna wa zamalimidwe, ulimi wamthirira ndi chitukuko cha madzi udatsimikiza za mliriwu womwe akuti udasautsa pamalo ena osambitsirapo ngombe a Mthumba omwe ali mgawo loyanganira za ulimi la Mitole EPA. +Mchikalata chomwe Maganga adasayinira sabata yatha, undunawu udati chigodola cha ngombe ndi nthenda yovuta kwambiri ndipo imagwira ziweto monga ngombe, mbuzi, nkhosa ndi nkhumba komanso nyama zakutchire monga njati. +Potsirapo ndemanga pamliriwu, wachiwiri kwa mkulu woyendetsa ntchito za zaumoyo wa ziweto ndi ulimi wa ziweto, Dr Patrick Chikungwa, adati nthendayi ndi yowopsa kwambiri ndipo ngati yalekereredwa imafala msanga. +Nthendayi imafala kudzera mumpweya, kukhudzana kapena kudya msipu womwe uli ndi tizilombo (virus) toyambitsa matendawa, adatero Chikungwa. Adaonjezera kunena kuti anthunso atha kufalitsa tizilombo ta nthendayi kudzera mzovala kapena nsapato, koma adati alimi asade nkhawa chifukwa boma likuchita zothekera kuti nthendayi isafalikire madera ena. +Iye adati zizindikiro za nthendayi ndi kuchucha malovu, matuza mkamwa komanso pakati pa zikanamba za miyendo zomwe zimapangitsa kuti ngombe izivutika poyenda. +Ngati mlimi aona zizindikirozi, chomwe ayenerea kuchita nkupatula ziweto zodwalazi kuti zisakhudzane ndi zimene sizinakhudziwe ndi nthendayi, Chikungwa adalangiza. +Mavuto osakata pa Wenela Tidakhala malo aja timakonda pa Wenela ndipo zidaonekeratu kuti zochita zikusowa. Kodi nkumachitanji pomwe zinthu zikukwera mtengo tsiku ndi tsiku ngati palibe womanga mabuleki? Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Musandiuze za Moya Pete chifukwa momwe ndidakuuzirani muja, palibe icho achita. Dziko lili pa auto pilot basi. +Nanga inu! Kusakaza nkhalango kwagundikaku mungati zinthu zikuyenda? Kodi nkhalango ndidaisiya kwathu kwa Kanduku lero ndingakaipeze pamene ootcha makala sakugona koma kusaka njira zothera mitengo kumeneko? Pamene nkhalango zikutha, Moya Pete akungoti asiya kugwirizana ndi awo ampalamatabwa, kuwaletsa kudula kesha ndi msetanyani? Nanga abale ake andale amene amatulutsa nkhuni, matabwa komanso mbande za mitengo akuwasiya bwanji? Aliyense akudziwa kuti Mowe Pati ali mgulumo. Mulinso uyu Mulibe wa galimoto zake. Nanga uja mbale wathu wosowa ya lendi mtauni Shati Choyamba wa ku Lower Shire! Onse akuwadziwa. +Nanganso bwanji osauza abale ake a Eisssshcom, inde anyamata oonetsetsa kuti kuzima kwa magetsi kukufalikira bwino, inde kampani yogulitsa mdima nawonso amakhapa mitengo ati akonze mapolo! Kodi mdima amagulitsa? Mukadzapeza munthu akugulitsa mdima, dziwani satana ali bwino. Inde, Dyabulosi akaona munthu wotere amavula chipewa nkugwada ndi kunena kuti: Dutsani amfumu. Inu ndi munthu wamkulu zedi, thambo la kumwamba ndi dziko lapansi zonse zilambira ufumu wanu. Kuguwa kwanu palibe angayerekeze kufikako. +Abale anzanga, nanga tsiku ndi tsiku, munthu wopuma, wa umunthu wake, angamasangalale kunena kuti lero ndizimitsa kuwala kuti akuba atambalale? Munthu wokhala ndi umoyo wauzimu nkumanyadira kuti timakanda tifera kumagetsi chifukwa cholephera ntchito? Zamanyazi. +Chilichonse sichikuyenda. +Nanga Adona Hilida ndiye ali kuti? Kuthawa pano pa Wenela mopanda mantha, mayi uyu ali ndi mafunso akuti ayankhe. +Nanga mwaiwala kuti iyeyo ndiye adanena kuti: Amene adaombera Yomphwi ndikuwadziwa. Ndipo awo adasolola makobidi nkundigawira ndi zawo. Wakudya nawo alibe mlandu. +Zoti ameneyu ndiye ankatsogolera tonse ojiya, osolola ndi osenza pano pa Wenela? Kodi iyeyo ndi Abiti Patuma bola ndani? Ndipo pomwe ndikukuuzani nkhaniyi, mbale wake Oswin Pitapo akuyembekezera kulandira udotolo wake. Ndangomva kale kuti atatsindika kuti palibe katakwe ngati iye posolola, sukulu yaukachenjede kuja kwa Chikanda ku Zomba Lachisanu imayembekezera kumupatsa udotolo wovuta. Ati iye ndi Doctor of Philosophy in Colossal Tax Payer Pilferage of Extraordinary Proportions. Dotolo wamkulu. Chifwamba. Tsinzinantole wamkulu. Wamtali zala wamkulu kuposa onse. Nyapala. Wandende. Kaidi Nanga ndatukwana? A Ndirande iyi! Machinjiri iyo! Lilongwe kwerani ka Starlet aka mukafika! ndidakuwa. +Samalani: Kwabuka matenda a chimanga Boma liletsa kugula mbewuyi mmaiko akunja okhudzidwa Chilinganizo cha boma choletsa kugula chimanga mmaiko a South Sudan, Uganda, Kenya, DR Congo ndi Tanzania kaamba ka matenda a chimanga omwe abuka mmaikowo, sichidakomere ena mdziko muno ndipo apempha boma kuti lipeze njira zothandizira anthu kuti asafe ndi njala. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Popewa kulowetsa matenda a chimanga mdziko muno boma lati ndi bwino kugayitsiratu chimangacho komweko Boma laletsa kugula chimanga mmaiko akunja monga South Sudan, Uganda, Kenya, Democratic Republic of Congo (DR Congo) ndi Tanzania kaamba ka matenda a chimanga amene abuka mmaikowo, koma lati amene akufuna kutero azingobweretsa ufa. +Mlembi wa unduna wa zamalimidwe, Erica Maganga, wati boma lapereka chiletsochi pofuna kutchinjiriza kuti matenda a chimanga amene abuka mmaikowo, otchedwa Lethal Necrosis, kuti asafalikire mdziko lino chifukwa ndi oopsa kwambiri. +Malinga ndi undunawu, matendawa akuononga chimanga koopsa ndipo mankhwala ake sadapezekebe. +Matenda a Lethal Necrosis amafalikira ndi tizilombo (viruses) kapena kubzala mbewu yomwe ili ndi matendawa komanso chimanga chomwe chakhudzidwa ndi matendawa. +Zina mwa zizindikiro za matendawa nkufa kwa chimanga chikangofika poti chayamba kutulutsa ngaiyaye. Ngati munda wakhudziwa, palibe chimanga chimene chimapulumuka, malinga ndi unduna wa zamalimidwe. +Undunawu wati padakalipano njira zothanirana ndi matendawa sizidapezeke kotero anthu akungoyenera kupewa kuti matendawa asafike mdziko muno. +Ngati mwagula chimanga kumaiko okhudzidwawo, chigayitseni komweko musanalowe nacho mdziko muno, adaunikira Maganga. +Koma ngakhale chiletsochi chadza pofuna kuti matendawa asafalikire mdziko muno, anthu amene akupulumira chimanga cha mmaiko akunja monga ku Tanzania ati ali ndi mantha kuti afa ndi njala chifukwa amadalira chimanga chomwecho malinga nkuti dziko lino silidakolole chokwanira chaka chino. +Senior Chief Kabunduli wa mboma la Nkhata Bay, wauza Tamvani kuti mbomalo muli njala ndipo anthu akupulumukira chimanga chochokera ku Tanzania poti mmisika ya Admarc akuti mulibe chilichonse. +Tikadya ndiye kuti takagula chimanga ku Tanzania. Ngati boma likuti tisakagule chimanga ku Tanzania, ndiyetu tifa ndi njala, adatero Kabunduli. +Mwana ukamuletsa kuti usakadikize khomo ilo, ndiye kuti kholo limayenera limupatse chakudya. Ngati boma likutiletsa kugula chimanga ku Tanzania, likuyenera litipatse chakudya. Monga ndanena, ku Admarc kulibe kanthu ndiye titani? Maganga adati ngati munthu akufuna kugula chimanga kuchokera kunja ayenera atenge chilolezo kuchokera kunthambi ya kafukufuku wa mbewu ya Chitedze Agriculture Research Station ku Lilongwe asadapite kukatenga chimangacho, mfundo yomwe Kambunduli akuti ikhala yovuta. +Mundiuza kuti munthu achoke kuno kapena ku Nsanje ulendo ku Chitedze kukatenga chilolezo ndiye abwerere kukagula chimanga? Ndalama yake iti? adatero Kabunduli. +Malinga ndi njala yomwe yavuta mdziko muno, boma lidalengeza kuti likufuna ligule pafupifupi matani 100 000 a chimanga kuti pasapezeke munthu wofa ndi njala. +Padakalipano boma lili kalikiriki kugula chimanga mmaiko a Zambia ndi Tanzania ndipo, malinga ndi wailesi ya boma ya MBC, pofika sabata yatha nkuti matani 10 000 a chimanga atalowa kale mdziko muno kuchokera ku Zambia pa matani 35 000 omwe ligule kuchokera kudzikolo. +Nanga zikutheka bwanji kuti boma likuitanitsa chimanga kumaiko akunja, monga ku Tanzania, pomwe likuletsa ena kuti asatero? Maganga adati timutumizire mafunso koma kuchoka Lolemba mpaka tsiku lomwe tinkasindiza nkhaniyi adali asanatiyankhe. +Chotsani ndale mu ulimi wamthiriraJalavikuba Inkosi Jalavikuba ya mboma la Mzimba yapempha boma kuika alimi patsogolo ndi kuchotsa ndale muulimi wamthirira. +Mfumuyi idanena izi Loweruka lapitali mdera la kumpoto mboma la Mzimba pachionetsero cha ulimi wamthirira pomwenso idawapepesa alimiwa ati chifukwa salabadiridwa. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Jalavikuba adati chifukwa boma lalowetsapo ndale paulimi wamthirira, ulimiwu sukupita patsogolo. Ndale, iye adati, zikulowa pa momwe kontilakiti zomangira masikimu a mthirira zikuperekedwera. +Ndale zatisaukitsa, atsogoleri andale, amipingo ndi ife mafumu tiyeni tisiye ndale ndi kuchita chitukuko. Atolankhani mukanene chilungamo, ine si wandale, adatero Jalavikuba. +Iye adati ndi zomvetsa chisoni kuti ngakhale dziko lino limadalira ulimi pachuma chake, boma silikuikapo mtima kwambiri. +Alimi paokha akuyesetsa, mbali yatsala ndi ya boma kuti liziwapatsa thandizo loyenera, iye adatero. +Jalavikuba adakumbutsanso alimiwo kuti ulimi ndi bizinesi ndipo aziikirapo khama. +Koma alimiwo adadandaula kuti ulimi wamthirirawu akuumva kuwawa kaamba ka ngalande zomwe sizikugwiritsidwa ntchito chimangireni. +Iwo adati yemwe adamanga ngalandezo adamanga mwachinyengo moti zina zidagumuka chifukwa chochepa simenti, pamene zina sizitha kuthirira minda chifukwa zili mmunsi kwambiri. +Mmodzi mwa alimiwo, Austin Chavula, yemwe ndi wapampando wa sikimu ya Ndau, adati boma likufunika liunikenso momwe ntchitoyo adayigwirira. +Povomerezana ndi Chavula, Edward Mvula, wapampando wa sikimu ya Chanolo, adati alimiwa akusowa pogwira ngakhale boma lidaononga ndalama zankhaninkhani pokumbitsa ngalande mchaka cha 2011. +Pakadalipano tikupempha boma litiganizire potipatsa simenti yokonzeranso ngalandezi kuti mthirira uyende bwino, Chavula adatero. +Ndipo wachiwiri kwa wapampando wa komiti ya Nyumba ya Malamulo pazaulimi, Joseph Chidanti Malunga, adati komiti yake ipereka madandaulowo kuboma ndipo akukhulupirira kuti lichita kafukufuku pankhaniyi. +Malunga, yemwenso ndi phungu wa Nyumba ya Malamulo mdera la kummwera cha kumadzulo mboma la Nsanje, adati nzodabwitsa kuti dziko lino likuitanitsa chakudya kunja pamene lili ndi kuthekera kodzilimira. +Ngati boma lingaike mtima powapatsa anthu zipangizo zowayenereza paulimi, sindikuona chifukwa chogulira chimanga kumaiko ena, Malunga adatero. +Iye adati chofunika ndi kudzikonzekeretsa poika ndondomeko zogwirizana ndi momwe zinthu zikuyendera. +Ndipo Agnes Nyalonje, phungu wa derali yemwe adakonza chionetserocho, adati dera lake lili ndi kuthekera kodyetsa gawo lalikulu la dziko lino. +Lipy G: Woimba za chinyamata Masiku ano kwadza oimba achinyamata amene akumaimba nyimbo zawo zothamanga kwambiri. Kulitu anyamata monga Nepman, Blasto, Piksy ndi ena otero amene lusoli lakhazikika. Komansotu kuli anyamata ena amene akuonetsa kuti ataikapo mtima akhoza kusadabuza izi. Awa ndi monga Lipy G, amene adacheza ndi CHIMWEMWE SEFASI motere: Ndikudziwe Dzina langa lenileni ndi Edward Fortiner, ndine wachiwiri kubadwa mbanja la ana 6. Ndimachokera chigawo chakumwera mboma la Nsanje. +Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Lipy G: Ena amatipondeleza Kodi kuimba zadansi udayamba liti? Kuimba ndidayamba pakale ndithu, nthawi imeneyo ndili kusukulu ya sekondale, ndi pamene ndimazindikira kuti ndili ndi luso losangalatsa anthu kupyolera mmaimbidwe , munyimbo za dansi. +Kodi ndi chani chomwe unapindulako kuchoka maimbidwe? Ine kudzera mmaimbidwe malinga ndi ndalama zomwe ndimapeza kuchoka ku zoimbaimba zandithandiza kwambiri moti pano ndinatsegula malo wojambulira nyimbo amene amatchuka ndi dzina loti Future Records. Uku ndi ku Zingwangwa mumzinda wa Blanytre. +Kupatula kuimba umachitanso chiyani pamoyo wako wa tsiku ndi tsiku? Inetu ndimapanga bizinesi komanso ndine katswiri pankhani yojambula nyimbo. +Kodi chimbale chako chatsopano chituluka liti? Mutu wake ndi chani? Chimbale changa chikuyembezereka kutuka mapeto a mwezi wa October, chomwe chikhale ndi nyimbo zokwana khumi zomwe zayimbidwa mu chiyakhulo cha Chichewa ndi muchizungu. Ndipo kuyambira pa 15 October 2015 mpomwe ndiwadziwitse Amalawi zambiri. +Kodi ndi mavuto ati omwe oimba zadansinu mumakumana nawo? Mavuto omwe timakumana nawo ndi monga kupita kuzoimbaimba koma osapatsidwa ndalama yomwe tidagwirizana, kumeneku ife timaona ngati tikuponderezedwa komanso anthu ena kuti atukule luso lathu amafuna kuti tiwapatse ndalama. +Kodi ndi anthu ati omwe unaimbako nawo nyimbo limodzi chiyambireni kuimba pa Malawi pano? Inetu chiyambireni kuimba pa Malawi pano ndiyimbako nyimbo ndi anthu ambiri monga Blasto, Nepman. Awa ndi akadaulo komanso ndaimbako maiko akunja monga Botswana, south Africa ndi Uganda. +Pomaliza tandiuze zomwe umakonda. +Bullets yayamba ndi ukali Timu ya Big Bullets, yomwe ikuteteza chikho cha TNM Super League, yayambanso ndi ukali mndime yachiwiri ya ligiyi, kupitiriza zomwe idachita mndime yoyamba. +Timuyi idachapa Mafco ku Dwangwa komwe ndime yachiwiri ya ligiyi idakakhazikitsidwa. Bullets idapambana 1-0 ndipo pano yaonjezera mapointi kufika pa 35. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Bullets ili ndi mapointi 7 pamwamba pa Azam Tigers, yomwe ili ndi mapointi 28. Koma Azam yamenya magemu ochuluka ndi imodzi kuyerekeza Bullets. +Azam idalepherana mphamvu ndi Kamuzu Barracks komanso Epac FC kuti ibwerere ku Blantyre ndi mapointi awiri kuchokera ku Lilongwe. +Mmodzi wa makochi a timu ya Bullets, Mabvuto Lungu, adati chomwe akufuna kuchita nkuteteza mbiri yawo yosagonja. +Bullets sidagonjepo mndime yoyamba ya ligiyi. +Matimu onse akonzekera zofuna kugonjetsa Bullets, ndipo akubwera mokonzeka kuti akwaniritse zomwe akufuna. Komabe tiyesetsa kuti mbiri yathu isasinthe, adatero Lungu pouza Tamvani. +Mawa timuyi iswana ndi Red Lions pa Kamuzu Stadium. Mndime yoyamba Bullets idalepherana mphamvu ndi timuyi 1-1 ku Zomba. +Timu yomwe Bullets imalimbirana nayo ufumu mumzinda wa Blantyre, Mighty Be Forward Wanderers, yayamba moipa mmdimeyi pamene idagonja ndi Civo United 1-0 pa Kamuzu Stadium sabata yatha. +Lero Wanderers, yomwe ili ndi mapointi 26, ndipo ili pa nambala 5, pamndandanda wa momwe matimu akuchitira mligiyi, ichapana ndi Kamuzu Barracks, yomwe ili ndi mapointi 23. Masewerowo ali pa Kamuzu Stadium. +Matimu ena amene ayamba molakwika ndi Dedza Young Soccer, yomwe idagonja ndi Red Lions. Mawa Young Soccer ndi Silver Strikers pa Silver Stadium. +Anyamata a ku Dedzawa ali panambala 11 ndi mapointi 15. +FISD Wizards nayo yayamba ndi kulira pamene idaswedwa ndi Civo 1-0 pa Kamuzu Stadium. Lero FISD itengetsana ndi Moyale ku Mzuzu ndipo mawa ikutikitana ndi Mzuni FC pabwalo lomwelo. +FISD ili kunsonga kwa ligiyi ndi mapointi 9 okha. Mzuni ili panambala 15 ndi mapointi 11 pamene Moyale ili pa nambala 10 ndi mapointi 19. Mzuni ndi Moyale onse adaswedwa ndi Silver sabata yathayi. +Nayo Airborne Rangers idathotholedwa nthenga nkugwa itatibulidwa ndi Blue Eagles 3-0. Lero Airborne ikulandira Epac ku Dwangwa pa Chitowe. Timuyi ili ndi mapointi 13 ndipo ili panambala 12, pamene Epac ili panambala 13 ndi mapointi 12. +Lero maso akhale pa Kamuzu Stadium ngati Bullets ipitirire kuchita bwino pamene ikuswana ndi mikango ya ku Zomba, Red Lions. +Siyayo Mkandawire atisiya Thambo lagwa kubanja la a Mkandawire a mmudzi wa Zebera mdera la Mfumu Yaikulu Mmbwelwa mboma la Mzimba komwe akulira imfa ya Siyayo Mkandawire, kholo lomwe akhala akulidalira muzonse. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Kadimba Mkandawire, yemwe ndi mmodzi mwa ana malmuyu, adati bambo awo adamwalira mbandakucha wa Loweruka lathali atadwala nthawi yaitali. +Siyayo Mkandawire adatchuka kwambiri ndi gule wa vimbuza makamaka munthawi ya ulamuliro wa malemu Kamuzu Banda. +Ndipo ndi thandizo la Kamuzu Banda, Mkandawire adalembedwa ntchito mboma komanso adayenda maiko ambiri kukasangalatsa anthu ndi mavinidwe ochititsa chidwi. +Ndi zachisoni kwmbiri kuti tsopano tatseka mbiri ya madalawa pomwe taika thupi mmanda. Banja lathu lataya kholo lomwe limatithandiza muzambiri. Awa ndi madala omwe adatsalapo odziwa chikhalidwe chathu ndipo amayesetsa kutiphunzitsa tonse, Kadimba adauza Tamvani kudzera pa lamya Lamulungu lapitali. +Koma mkuluyu adatsindika kuti izi sizikutanthauza kutha kwa gule wa vimbuza. +Kadimba adati iye ndi wokonzeka kupitiriza pomwe bambo awo adasiyira ncholinga cholimbikitsa chikhalidwe chawo. +Mwambo woika maliro a khanda lozizira Amalawi ngakhale ali ndi miyambo yosiyanasiyana malinga ndi mitundu yawo monga Achewa, Angoni, Atumbuka, Alhomwe, Amanganga, Asena kaya ndi Ayao, koma pamwambo woika khanda lopitirira zochitika zimakhala zofanana. DAILES BANDA adacheza ndi mayi Catherine Ligowe kuti afotokoze mmene mwambo woika khanda lozizira umayendera. Adacheza motere: Ndikudziweni mayi wanga. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Ndine Catherine Ligowe. Ndidabadwa zaka zambiri zapitazo. Ndimachokera ku Ntcheu mmudzi mwa Chikadya, T/A Ganya. Ndili ndi ana asanu ndi awiri. Ndinenso namkungwi kumudzi kwathu komanso ndidali mzamba. +Kuno ku Mzuzu mukupezekako bwanji? Mavuto mwanawe. Kuyeseyesa kuti tipezeko koponyako mkamwamu. +Ku Mzuzu kunonso ndinu namkungwi? Ayi, ku Mzuzu kuno unamkungwi wanga umakhala wa mmakwalalamu koma kumudzi ndi komwe ndimagwira ntchitoyi kuchinamwali, tere chaka chomwechi ndidali komweko. +Mutiuzeko pangono za maliro akhanda lopitirira Inu mufuna mudziwe chani? Tiyambe ndi mwambo wa maliro mmene umakhalira. +Khanda lopitirira limatchedwa kuti khanda lozizira chifukwa mayi a khanda lija amakhala kuti sadakhale kaye pamodzi ndi mwamuna. +Mukutanthauza kuti khanda litamwalira pamiyezi iwiri makolo ake asadakhalire malo amodzi mwambo wake umakhala ngati wa khanda lopitilira? Eya, chifukwa timakhulupirira kuti mwanayo sadatenthetsedwe ndi bambo ake. +Zimayenda bwanji? Mwana uja akamwalira amakaikidwa ndi azimayi okhaokha koma azimayi aja saloledwa kulira malirowo chifukwa kulira kuja kumachititsa kuti mayi uja asadzaberekenso. Manda a malirowa sakhala akuya ngati a maliro a munthu wamkulu. +Chifukwa chiyani sakhala akuya? Kalekalelo makolo athu ankakhulupirira kuti manda a khanda lozizira akakhala akuya kwambiri mayi wa khandalo sadzaberekanso. +Ndiye maliro a mapasa mumachita bwanji? Akamwalira mmodzi mwa ana amapasa azimayi akalira malirowa timakhulupirira kuti mwana wotsala uja amamwaliranso, komanso tikamaika malirowa timaika khanda lomwaliralo ndi mvunguti pambali pake kuti mzimu wake uziona ngati akadali ndi mnzake uja. +Nanga wotsalayo mumatani naye? Ameneyo timamusambitsa mumankhwala kuti mzimu wa mnzake uja usamamubwerere. +Tsopano inu mumati mudali mzamba, mudabadwitsako mwana wopitirira? Ayi, palibe mwana wopitirira amene ndidabadwitsako. +Mudasiyiranji ntchitoyi? Boma lidaletsa komanso anthu amene amabereketsa azimayi amafa maso nchifukwa chake anamwino ambiri ochiritsa azimayi kuchipatala amakhala ovala magalasi. Kalekalelo mzamba asadayambe kugwira ntchito amayamba kaye wasamba mankhwala kuti adziteteze ku ukhungu. +Chimachititsa kufa masoko ndi chiyani? Chimachitika ndi chakuti azimayi akamabereka amachita zinthu zodabwitsa zambiri ndiye ukaona zinthu zimenezo kwanthawi yaitali maso aja amafa, umangoona zinthu mwa mbuu. +Zikomo kwambiri chifukwa cha nthawi yanu. +Zikomo. +Mkulu wa zaka 22 akaseweza zaka 23 Wakhala akuthyola nyumba masana kasanu konse ndi kubamo katundu. Anthu ku Balaka akhala akumusaka koma adali woterera ngati mlamba. Koma la 40 lamukwanira John Bunaya, wa zaka 22, amene bwalo la milandu lamuthowa ndi zaka 23 kuti akaseweze kundende chifukwa cha kutolatola. +Wapolisi woimira boma pamilandu, Inspector Isaac Mponela, wati bwalo la Balaka lidapeza mkuluyu wolakwa pamilandu yonse isanu yomwe adapalamula. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mponela adauza bwalolo kuti pa 3 March, chaka chino, masanasana dzuwa likuswa mtengo, Bunaya adaswa nyumba ya Gloria Mphwiyo ndi kubamo njinga ya komanso matumba awiri a chimanga. Zonse zidali za mtengo wa K43 000. +Pa 28 March, chaka chonchino, Bunaya akutinso masanasana adaswa nyumba ya Ruth Marley ku Majiga mbomalo ndi kubamo wailesi komaso zovala ndi katundu wina. +Bunaya pa 13 April, akuti adaphwanyanso nyumba ya Rachel Jika ndi kubamo laputopu, matilesi, mafuta ophikira ndi shuga za K320 000. +Pa 10 May, Bunaya akuti adaswa nyumba ya William Munthali ndi kubamo kamera, foni ndi zakugolosale za K72 000. +Iye sadalekere pomwepo. Pa 13 May akuti njondayi idakaswanso nyumba ya Daniel Pondani komwe adakasokolotsa DVD, masipika awiri a LG, mafuta ophikira ndi mafoni za K100 000. +Mponela atamaliza kumunenera Bunaya kubwaloko, anthu adadzidzimuka. Izi zidadabwitsanso woweruza milandu, Victor Sibu, yemwe sadachedwe koma kusatakula chilango chokhwima. +Iye adalamula Bunaya, yemwe adavomera kulakwa pamilandu yonseyi, kuti akaseweze zaka 23 ngakhale iye adaliralira kuti ndi wachichepere komanso ndiye amasamala banja lake ndi makolo omwe adati ndi okalamba. +Bunaya amachokera mmudzi mwa Kandengwe kwa T/A Nsamala mbomalo. +Chikondi chidayambira kuubwana Akuti chikondi chidayambira kuumwana kalelo pomwe ankasewerera limodzi nkumakula pa Kalera ku Salima ndipo lero akhala thupi limodzi. +Francis Tayanjah-Phiri, mtolankhani wodziwika bwino yemwe akugwira ntchito kukampani ya Times Group, sabata yathayi adamanga chinkhoswe ndi nthiti yake, Stella Kamndaya, yemwe ndi mphunzitsi ku Lumbadzi mboma la Dowa. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Tayanjah ndi dona wake Stella kugonekerana khosi patsiku la chinkhoswe Tayanjah adati mzaka za mma 1980 mayi ake ankaphunzitsa pasukulu ya pulayimale ya Kalera limodzi ndi bambo ake a Stella ndipo mabanja awiriwa adali pachinzake cha ponda-apa-nane-mpondepo, zomwe zidabzala mbewu ya chikondi mwa ana awo. +Pa anzanga onse yemwe ndinkagwirizana naye kwambiri adali iyeyu kufikira pomwe ndidapita kukapanga maphunziro a utolankhani ndipo naye adakapanga kozi ya uphunzitsi. Kuyambira pamenepo tinkangomva kuti wina ali uku ndipo wina ali uku, adatero Tayanjah. +Iye adati kutalikiranako sikudafufute chikondi chomwe adali nacho pakati pa wina ndi mnzake ndipo ankaganiziranabe nthawi zonse mpakana mwamwayi adakumana aliyense akuyendera zake mumzinda wa Lilongwe, nkukumbukira kale lawo. +Chifukwa cha chikumbumtima cha kale lathu, titakumana padalibe chilendo chilichonse ndipo tidayambiranso kucheza, koma ndidaona kuti ubale womwe adatiphunzitsa makolo athu kalelo tiuonetsere kudziko, adatero Tayanjah. +Iye adati nyengo ikupita ndi machezawo adapereka maganizo a banja ndipo mtima wake udadzadza ndi chimwemwe choopsa Stella atavomera. +Naye Stella adati kwa iye adali ngati maloto okoma oti ukadzuka zomwe umalotazo zikuchitikadi uli maso. +Ndidalibe chifukwa chotengera nthawi kuti ndikaganize kapena kuti ndimuone kaye chifukwa ndakula naye ndipo nzeru zake, khalidwe lake, chikondi chake zonse ndidali ndikudziwa kale kuchokera tili ana, adatero Stella. +Iye adati ali ndi chiyembekezo cha banja lapamwamba ndi Tayanjah ndipo pemphero lake ndi lakuti Mulungu awapatse luntha lomwe adapatsa makolo awo pakasungidwe ka banja ndi kaleredwe ka ana. +Tayanjah amachokera mmudzi mwa Rubeni, T/A Kambwiri ku Salima ndipo Stella kwawo ndi kwa Daniel, T/A Maganga ku Salima komweko. +OPEZEKA KUMANDA AYANKHA MLANDU Anthu a mmudzi mwa Yesaya Nkosi Mfumu kwa Inkosi Chindi mboma la Mzimba adadzidzimuka ataona galimoto yachilendo itaimitsidwa pamanda a mmudzimo pomwe anthu anayi adali kuchita chizimba kumandako. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Mneneri wa polisi mboma la Mzimba, Gabriel Chiona, adatsimikiza za nkhaniyi ponena kuti iwo adanjata anthu anayi omwe akuganiziridwa mlandu wokhala pamalo popanda chilolezo ndipo iwo adakaonekera kubwalo la milandu la majisitireti Lachinayi pa 20 August. +Chiona adati anthuwo ndi Koloboyi Mwazembe, wa zaka 35, wochokera mboma la Chitipa; Esau Simwimba, wazaka 36, wochokeranso ku Chitipa; Tenson Mhone, wa zaka 65; ndi Chrissy Phiri, wa zaka 73, onse a mboma la Mzimba. +Malinga ndi Chiona, Mwazembe ndi Simwimba alamulidwa kukakhala kundende kwa chaka chimodzi kapena apereke chindapusa cha K90 000 atawapeza olakwa pamlandu wopezeka kumanda popanda chilolezo. +Koma Phiri ndi Mhone adzalowanso mbwaloli sabata ino kuti adzayankhe milandu yopezeka pamalo popanda chilolezo komanso kuba mwachinyengo, milandu yomwe iwo aikana. +Chiona adati anthuwo adanjatidwa pa 13 August pomwe mfumu Msipani Nyirenda adauza apolisi za anthu omwe adali kumanda a mmudzimo. +Malinga ndi Chiona, bambo wina adaona galimo ya oganiziridwawo itaima kwa nthawi yaitali pafupi ndi manda a mmudzimo, zomwe zidamuchititsa kuti akanene za nkhaniyi kwa nyakwawa yemwe adatsina khutu apolisi. +Anthu a mmudzimo adawagwira oganiziridwawo panthawi yomwe amatuluka kumanda. Mmodzi mwa oganiziridwawo adanyamula chithumwa, komanso adapezeka ndi ndalama zokwana K700 000, adatero Chiona. +Msangulutso utafunsa mmodzi mwa oganiziridwawa, Phiri, kuti afokotokoze zomwe ankachitika kumandako, iye adati amafuna chizimba cha bizinesi ndipo chithumwa chomwe adali nacho nchokawira anthu ndalama. +Chithumwachi chimakawa anthu ndalama. Muli njoka yomwe imakhala ikukawa anthuwa ndalamazo, adatero Phiri. +Phiri adati bambo wina adagula njoka kwa singanga, Mhone, yomwe imakawa anthu ndalama koma njokayo idathawa. Iye adati njokayo itathawa iye adaganiza zokagula ina yomwe singangayo adati idali kumanda komwe adapezekako. +Khansala wa derali, Dan Nkosi, adathirira ndemanga za nkhaniyi ponena kuti apolisi adabwera kunyumba kwakwe kudzamutenga kuti akaone zomwe zidachitikazo. +Ndidapeza anthu atawagwira oganiziridwawo kupita nawo kwa mfumu Msipani Nyirenda komwe adafunsidwa zomwe amachita. Iwo adafotokoza kuti amagulitsana chizimba pamtengo wa K700 000 chomwe tidawapeza nacho, adatero Nkosi kuuza Msangulutso. +Mfumu Msipani Nyirenda sadathe kupezeka kuti ayankhulepo pankhaniyi. +A khonsolo ndi ankhanzaAmalonda Ena mwa ochita malonda (mavenda) mmisewu ya mumzinda wa Blantyre alira ndi khalidwe la akhonsolo ya mzindawu kuti akuwachitira nkhanza ngati Malawi si dziko lawo. +Pocheza ndi Msangulutso mavendawa akuti akupempha khonsoloyi kuti iwaganizire, maka iwo amene akuchita mabizinesi angonoangono. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Koma mneneri wa khonsoloyi, Anthony Kasunda, akuti sadalandirepo dandaulo lililonse kuchokera kwa anthuwa. Iye wati zomwe akudziwa nzoti akhonsolowa akumamenyedwa ndi mavenda akamagwira ntchito yawo yoletsa malonda mmalo amene si oyenera kuchitiramo bizinesi. +Tikudziwa kuti nthawi zambiri ma rangers (othamangitsa anthu mmalo oletsedwa) athu akhala akugendedwa ndi mavenda ndipo umboni ulipo chifukwa timapita nawo kuchipatala. +Galimoto zathunso zagendedwapo kambirimbiri. Mukumbukira kuti ranger wathu wachikazi adamenyedwa mu Limbe ndi ochita malonda koma anthu anaona ngati kuti wamenyedwa ndi venda, adatero Kasunda. +Komabe amalondawa akuti akhala akudandaulira khonsoloyi koma sichitapo kanthu. +Francis James, amene amagulitsa mkaka wamadzi wa mmapaketi) adati adamenyedwapo ndi akhonsolowa komanso kumulipitsa K5 000 kaamba kochita malonda mumzindawu. +Adandigwira madzulo ndikupita kunyumba. Mmanja mwanga ndidali ndi machubu awiri a mkaka. Adandigwira ndi kundimenya ndi zitsulo mmiyendomu ndipo adandilipiritsa K5 000, adatero James. +Iye akuti akukumbukiranso za mnzake wina amene ankagulitsa nsapato. Adamulanda nsapato zonse ndipo patadutsa sabata, tidakumana ndi mmodzi mwa amene adamulandawo atavala imodzi mwa nsapatozo. +Mnzanga wina wogulitsa maheu adamumenyanso ndi zitsulo komanso adamumwera maheuwo, adatero James. +Naye mayi wina, yemwe adati ndi Alinafe, akuti adamugwira ndipo adakamutsitsa ku Chileka kuti akayende wapansi kuchokera kumeneko atamugwira ndi malonda a nthochi. +Koma Kasunda akuti katundu aliyense akuyenera kugulitsidwa mmalo ovomerezedwa ndi khonsolo kukhala msika. +Malo oyenera kuchita malonda ndi okhawo omwe khonsolo idakhazikitsa ngati msika, komanso malo amene avomerezedwa ndi khonsolo potsatira pempho lochokera kwa ofuna kuchita malonda. +Dziwani kuti aliyense wochita malonda malo amene khonsolo lavomereza amakhala ndi chiphaso, adatero Kasunda. +Moto buu! Ku Swaziland Kochi wa timu ya dziko lino ya Malawi Flames, Ernest Mtawali, wati timu yake yakonzeka kuonetsa zakuda timu ya Swaziland yomwe aphane nayo mumpikisano wa Africa Cup of Nations (Afcon) mawa lino pa Somhlolo Stadium mumzinda wa Lobamba. +Malawi ili mgulu L momwe muli Swaziland, Guinea ndi Zimbabwe. Awa ndi masewero achiwiri a Flames mumpikisanowu chigonjerreni 2-1 ndi ndi Zimbabwe pa Kamuzu Stadium pa 13 June chaka chino. Panthawiyo kochi adali Young Chimodzi, yemwe adachotsedwa ntchito kaamba ka kugonjaku. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Koma Mtawali akuti anyamata ake ali bwino ndipo akuyembekezera kuphophola Swaziland, timu yomwe mmasewero ake oyamba idakatikita Guinea kwawo komwe. +Ndili ndi chikhulupiriro mwa anyamata amene ndawatenga. Tikufuna kumwetsa zigoli chifukwa njira yabwino yoteteza golo lanu ndi kumenyera mpira kutsogolo kuti tikapeze zigoli, adatero mmene ankanyamuka mdziko muno Lamulungu lapitali kupita ku South Africa komwe idalepherana ndi Mbombela United 2-2 pamasewero apaubale pokonzekera Swaziland. +Malawi yakumanapo ndi Swaziland maulendo 18 ndipo yapambana katatu, kugonja ka 10 ndi kulepherana mphamvu kasanu. +Mumpikisanowu chaka chatha Malawi sidachite bwino pamene idakumana ndi matimu akuluakulu mgulu lawo monga Algeria, Mali ndi Ethiopia. Pamasewero onsewo, Malawi idangokwanitsa kupeza mapointi 7 itapha Mali pakhomo komanso Ethiopia ndi kulepherana ndi Ethiopia kwawo. +Koma Mtawali akuti timu yomwe ali nayo pano ndi ina ndipo chiyembekezo chilipo kuti mawa alandira zotsatira zabwino kuchokera kwa anyamata ake. +Mtawali watenga Limbikani Mzava, Stanly Sanudi, Yamikani Fodya, Wonder Jeremani, John Lanjesi, Pilirani Zonda, Yamikani Chester, Isaac Kaliati, Chimango Kaira, Chawanangwa Kaonga, Chiukepo Msowoya, Muhammad Sulumba, Manase Chiyesa, Robin Ngalande, Robert Ngambi, John CJ Banda, Chikoti Chirwa, Micium Mhone, Gerald Phiri jnr Richard Chipuwa Bright Munthali. +Amkhalakale monga Joseph Kamwendo, Fischer Kondowe, Esau Kanyenda, Frank Banda, Lucky Malata, Harry Nyirenda, Zicco Mkanda, Atusaye Nyondo, MacDonald Harawa ndi Charles Swini atsala. +Masewero a Zimbabwe, Malawi idachinya kudzera mwa John Banda amene mawali akhalenso ndi ntchito yaikulu pakati pa Flames. +Anatchezera Banja lavuta Zikomo Anatchereza, Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ndine mayi wa zaka 30 ndipo ndili ndi ana atatu. Kumbuyo kunseku timakhala bwinobwino ngakhale ndimamva kuti amuna anga akuyenda ndi akazi ena. Zimandiwawa koma ndinalibe nazo ntchito. Mu 2014 anzanga omwe ndimayenda nawo onse adali ndi zibwenzi ngakhale adali pabanja ndipo ankandiuza kuti nane ndipeze chibwenzi chamseri koma ndimakana. Kenaka nanenso ndinapeza chibwenzi chamseri, koma amuna anga atadziwa anandimenya kangapo ndipo ndapitako kwathu kambirimbiri mpakana afika saizi yomawakana ana, ati si awo. Ndayesetsa kuwapepesa kunena chilungamo, koma sizikutheka. Tikangoyambana iwowa amanyoza ana anga. Ndiye nditani? Ndathedwa nzeru, Mzuzu Ku Mzuzuko, Zikomo pondilembera kundiuza nkhawa zanu. Mayi, mavuto enawa timachita kuwaputa dala ife amayi. Choyamba, kodi inu simunamvepo anthu akunena kuti mamveramvera amapasula banja? Ndi zimenezotu! China, munthu umadziwika ndi abwenzi amene umacheza nawo. Ngati umayenda ndi opemphera, nawe ndiye kuti ndi wopemphera; ukamayenda ndi olongolola, nawenso umakhala wolongolola; ukamakondana ndi wamiseche, nawenso ndiye kuti umakonda miseche; kaya wakuba nawenso wakubachoncho! Tsono inu mudasankha kuyenda ndi kucheza ndi anzanu oti ali pabanja koma zibwenzi zamseri bwee! Ndiye inu mumati mutani? Simukadachitira mwina, koma kupeza wanu basi! Nkutheka kuti amakuuzani zoti amuna anu ali ndi zibwenzi zamseri ndi anzanu omwewo, nanga inu munagwira nokha kuti akuyenda ndi uje ndi uje? Misechetu imeneyo. Amafuna kuti mukopeke ndipo nanu muyambe kuyenda njira zomwe amayenda anzanu mukunenawo. +Mukadakhala wozindikira si bwenzi mukunena kuti mutamva zoti amuna anu ali ndi zibwenzi zamseri mudalibe nazo ntchito. Chifukwa chiyani? Mukanawafunsa amuna anuwo kuti kodi zimene ndikumva zoti mukuyenda ndi amayi oyendayenda ndi zoona? osati zimene mudachita zotchalenja inunso popeza wanu mwamuna wamseri woyenda naye. Atambwali sametana paja! Lero ndi izo, banja lanu lagwedezeka, chikondi ndi kukhulupirirana zazilala. Taonani, amuna anu tsopano ayamba kukaika ngatidi ana anu atatu mudaberekeranawo ndi awodi. Anawo akula ndi chithunzithunzi chotani cha bamboo awo ngati akuwakana? Kuzunza ana osalakwa kumeneko. +Abwenzi ena ndi olakwitsa. Chonde, azimayi, onetsetsani kuti mukuyenda ndi anzanu oyenera, amakhalidwe abwino, aulemu wawo kuti mabanja anu akhalenso aulemu. Mukakhala mbanja zibwenzinso nzachiyani, abale? Kunja kuno kwaopsa. +Tsono mongokuthandizani pangono, ngati banja lanu lili ndi ankhonswe ndi bwino adziwe mavuto anu ndipo mwina akhoza kukuyanjanitsani kuti banja lanu liyambenso kuyenda bwino. Mwinanso ngati mudamanga kumpingo athanso kukuthandizani kumeneko, koma choyamba kwenikweni awirinu muyenera kukhala pansi ndi kupepesana kuchokera pansi pa mtima, maka inuyo chifukwa anzanu ndiwo adakulakwitsani kuti mupange zinthu zosafunika mbanja. +Amangidwa kaamba kobisa khanda Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Pamene amayi ena akukangana ndi amuna awo mmidzimu kufuna nsalu yalekaleka, amayi ena ndi pamene mwayi woterewu akumauseweretsa nkumataya ana oberekabereka nkuthiridwa maunyolo ndi apolisi. +Izi zikutsatira kumangidwa ndi kutsekeredwa mchitolokosi kwa mayi wa zaka 22 pomuganizira kuti adafuna kubisa khanda lomwe adabereka ku Dowa. +Wofalitsa nkhani za polisi mboma la Dowa, Richard Kaponda, wati mayiyu ndi Jenifer Wilson, wa mmudzi mwa Kamphelo mdera la T/A Mkukula mbomali. +Kaponda adati nkhaniyi idachitika pa 4 August chaka chino mmudzi mwa Kamphelo. +Nkhani, Malingana ndi Kaponda, ikuti mayiyu ankakhala ku Lilongwe ndi chemwali wake wamkulu ndipo ali komweko mwamuna wina adamuchimwitsa ndi kumupatsa pathupi. +Iye adaganiza zopita kwa makolo ake ku Dowa atalephera kuchotsa pakatipo ndipo atafika kumeneko sadadziwitse makolo ake za nkhaniyi ndipo amaphimba mimbayo kuti isaonekere kunja ndi anthu. +Pomwe nthawi idakwana yoti abereke, adapita pathengo lina loyandikira pomwe padali chulu ndipo adabereka mwana wamkazi koma adamutayira mdzenje pachulupo momwe munali chiswe chomwe chinayamba kuteketa mwanayo, adafotokoza Kaponda. +Iye adati khandalo lidayamba kulira ndipo anthu amene ankadutsa pafupi ndi chulucho ndi amene adamva kulirako ndipo adakatsina khutu mfumu ya mmudzimo, yomwe idakanena kwa apolisi. +Kaponda adafotokoza kuti mwanayo adamutengera kuchipatala chachikulu cha Dowa komwe adakamwalira ndi chibayo kaamba kozizira. +Mayiyu woganiziridwayu adamumanga kaamba koti amatulutsa magazi atakamupima kuchipatala, zomwe zidapangitsa amuganizire kuti adabereka ndi kutaya khanda lake mdzenjemo. +Mayiyu akuyembekezereka kukaonekera kubwalo la milandu posachedwapa komwe akayankhe mlandu wofuna kubisa khanda. +Moto lawilawi mu TNM Super League Ligi ya TNM yafika pa lekaleka pamene matimu ena akutenga mapointi ndipo ena kutaya mwachibwana pamene ligiyi tsopano yalowa sabata ya chinambala 22. +Timu ya Big Bullets yomwe idali timu yokhayo yomwe isadaone kugonja mligiyi yakumana ndi chakuda sabata yatha pamene idapunthidwa ndi asilikali a Airborne Rangers ku Dwangwa komwe Bullets idagonja 2-1. +Chisale watuluka nkumangidwanso Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Kugonjaku kumadza timuyi itatibulidwa ndi Civo United mchikho cha Standard Bank 2-1. Kodi minyamayi ipitiriranso mawa pamene timuyi ikusinjana ndi asilikali a Moyale? Technical director wa Bullets, Billy Tewesa, adati sakuonanso akugonja mmanja mwa Moyale ndipo wati okonda Bullets abwere kudzaonera masewerawo ndipo adzasamba mkaka. +Banja lathu lidazolowera kudyera nyama, ndiye apapa nyama inasowa ndipo timadyera masamba. Koma mukamadyera masamba si zitanthauza kuti simudzadyanso nyama. +Pamene padavuta pakonzedwa, chilichonse tsopano chili mchimake ndipo okonda Maule abwere Lamulungu ndipo adzamwa mkaka, adatero Tewesa. +Mphekesera zamveka kuti timuyi ikufuna kutenga mphunzitsi wakale wa timuyi Kinnah Phiri amene wangobwera kumene kuchokera ku South Africa. +Izi zikudza malinga ndi kugonjaku ndipo lingaliro ndi lakuti timuyi iteteze ligiyi yomwe akuitsogolera ndi mapointi 41 pamasewero 18 ndipo Mafco ndiyo ikutsatira ndi mapointi 34 mmasewero 20. +Lero masewero alipolipo pamene Azam Tigers iswane ndi Be Forward Wanderers pa Kamuzu Stadium. Mumzinda wa Lilongwenso ndiye muli fumbi pamene Civo United ipumunthane ndi Silver Strikers pa Civo. Red Lions yaitana Moyale pa Zomba lero ndipo Blue Eagles yaitananso Kamuzu Barracks pa Nankhaka. +Kulambira Kalonga Gawa Undi Tamvapo zambiri za mwambo wa Kulamba. Mongokumbutsana, Kulamba ndi mwambo womwe mafumu Achichewa mmaiko a Malawi, Mozambique ndi Zambia amapezerapo danga lokapereka uthenga wa mmene zinthu zikuyendera mmadera awo kwa mfumu yawo yaikulu, Kalonga Gawa Undi. Lero tati tisanthule zina ndi zina zomwe zimaloledwa kuchita ndi kusachita pamaso pa mfumu ya Achewayi. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Senior Chief Lukwa wa ku Kasungu kumwambo wa Kulamba wa chaka chino motere: Ndikudziweni mfumu. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Ine ndine Senior Chief Lukwa, mmodzi mwa mafumu akuluakulu pakati pa Achewa a ku Malawi ndipo ndimachokera mboma la Kasungu. +Tandifotokozerani zokhudza ulemu wa Kalonga Gawa Undi kuyambira mmene mumaperekera moni. +Kalonga Gawa Undi ndi mfumu yaikulu kwambiri pakati pa Achewa kotero kuti ulemu wonse womalizira pakati pa Achewa umayenera kupita kwa Kalonga Gawa Undi. Pachifukwa ichi, palibe munthu aliyense yemwe amaloledwa kugwirana chanza ndi Kalonga Gawa Undi pokhapokha kalongayo atayamba yekha kupereka mkono koma sayenera kukhudzidwa mwanjira iliyonse. +Nanga popereka mphatso kwa Kalonga Gawa Undi zimakhala bwanji? Uwu ndi mwambo wina wapadera womwe umafunika kusamala kwambiri. Popereka mphatso kwa Kalonga Gawa Undi munthu amayenera kuika mphatsoyo pansi kapena pagome lomwe lakhazikitsidwa mwini wake akuona. Akatero, imodzi mwa nduna zake za kalongayo amakatenga mphatsoyo nkukaika pamalo oyenera, osati kumupatsira mmanja, ayi. Nthawi zonse kumakumbuka kuti kalonga ndi munthu wamkulu. +Nanga pokumana ndi Kalonga Gawa Undi, munthu amayenera kutani? Pokumana ndi Kalonga Gawa Undi, munthu amayenera kukhala pansi chotambalala osati chokhwinyata, ayi. Ngakhale mipando itakhalapo yambiri motani munthu amayenera kukhala pansi pokhapokhapo ngati mwini wake kalongayo wakukakamiza kuti ukhale pampando. Ngati uli Mchewa weniweni, ngakhale Kalonga atakukakamiza chotani, umayenerabe kukana ndi kukhala pansi basi, koma nkofunika kukumbukira kutambalala, osapinda miyendo pamaso pa Kalonga Gawa Undi. +Nanga ungatani kuti Kalonga Gawa Undi akupatse mpata wolankhula naye? Funso limeneli limavuta nthawi zambiri chifukwa anthu amaona ngati Kalonga Gawa Undi amangolankhula chisawawa. Pomwe Kalonga waperekera mpata wolankhulana naye si pano ndipo ngati ukufuna kulankhula naye umayenera kuomba mmanja ndi kulankhula mokwenza mawu akuti: Yooh, Gawa! katatu ndipo ngati ali ndi mpata akhoza kukupatsa mwayi wolankhulana naye. +Nanga ngati mfumu yaikulu ya Achewa, ubale wake ndi wotani ndi gulewamkulu? Choyamba, gulewamkulu alibe mphamvu iliyonse kwa Kalonga Gawa Unidi, chimodzimodzinso naye, ngati kalonga, alibe nthawi yopanga za gulewamkulu. Ntchito imeneyi amalekera mafumu ake kuti aziyendetsa. Kalonga akamayenda amayenera kuzunguliridwa ndi mbumba zake (amai oimba nyimbo). +Nchifukwa chiyani mbumba, osati nduna? Pamwambo wa Achewa amayi ndiwo amakhala ndi mphamvu zosankha mfumu. Pachifukwachi, amayi amapatsidwa ulemu wapadera chifukwa popanda iwo kasankhidwe ka mfumu kamasokonekera. Kalonga Gawa Undi amadziwa zonsezi ndiye pofuna kulemekeza udindo womwe amayi ali nawo, nchifukwa amafuna kuti mbumba ndizo zizimuperekeza. +Anatchereza Amandimenya Anatchereza, Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ndine mtsikana wa zaka 19 ndipo ndili ndi bwenzi la zaka 21 yemwe ndili naye mwana mmodzi. Dandaulo langa ndi loti akandipeza ndikucheza ndi anyamata amandimenya ngakhale kuti sitinakwatirane. Koma iyeyo amachezanso ndi atsikana ena koma ine sindiyankhulapo kanthu. Nthawi ina adandimenya mpaka kukomoka. Nditani agogo anga? LWT, Chilobwe, Blantyre LWT, Ndamva vuto lako, mwana wanga. Kuchitirana nkhanza mbanja kaya pachibwenzi si chinthu chololedwa ngakhale pangono ndipo aliyense wochitira mnzake nkhanza zamtundu uliwonse akulakwira malamulo ndipo atasumiridwa ayenera kulangidwa ameneyo. Zimatheka bwanji kuti anthu okondana azichitirananso nkhanza pomenyana? Wachita bwino kubweretsa vuto lako poyera chifukwa alipo ena amene akumachitiridwa nkhanza ndi okondeka awo koma zimangothera mmimba, ati kumenyana ndi mankhwala a banja. Si zoona zimenezi. Tsono iwe utamenyedwa ndi bwenzi lakolo mpaka kukomoka basi udangokhala duu! Nawenso ndiye kuti ndi wopepera! Adzakuphatu ameneyo ukapanda kusamala naye. Zikadzachitikanso uyenera kukamuneneza kupolisi kapena kumabungwe amene amayanganira za maufulu a anthu kuti adzakuthandize chifukwa akukuphwanyira ufulu wako ameneyo. Nditengerepo mwayi wolangiza achinyamata kuti kukhala ndi ana musadalowe mbanja zotsatira zake zimakhala ngati zimenezi. Chibwana basi! Zichepe chonde. +Ndikumukondabe Zikomo Anatchereza, Ndine bambo wa zaka 30 ndipo ndili ndi ana awiri. Vuto lomwe ndili nalo ndi loti mkazi ndinabereka naye ana anandithawa miyezi 11 yapitayo ati ndimamuvutitsa. Pakalipano ndapeza mkazi wa zaka 20 ndipo akunetsa kuti amandikonda. Ndinamuuza chilungamo chonse chokhudzana ndi ana ndipo adamvetsa. Ndithandizeni maganizo poti wakaleyo ndimamukondabe limodzi ndi ana anga. Koma wapanopayunso ali ndi pathupi panga. Ndithandizeni chonde. +ZTB ZTB, Nkhani yanu ndi yovuta ndipo sindidziwa kuti ndikuthandizani bwanji. Choyamba mwanena kuti mkazi wanu woyamba amene muli naye ana awiri adakuthawani chifukwa ati ndinu wovuta. Kuvuta kwake kotani? Inu mukuti mumamukondabe ndi ana, koma pano mulinso pachibwenzi ndi mayi wa zaka 20, yemwe pano ndo woyembekezera. Mafunso nawa: Ngati mkazi adakuthawaniyo mumamukondadi, mudachitaponji kuti mubwererane? Ngati mumamukondadi, chidachitika nchiyani kuti mugwenso mchikondi ndi mtsikana wa zaka 20 mpakana kumupatsa pathupi musanamukwatire? Chimene ndikuona apa ndi chinyengo kumbali yanu ndipo ndinu wovutadi abambo inu. Ndinu wachimasomaso ntheradi! Poti munthu sudziloza chala, mwina mkazi wanu woyambayo adaona kuti ndinu wovuta ndi nkhani yokonda akazi koma muli pabanja. Tsono ngakhale mutabwererana ndi mkazi adathawayo, nanga mwana wa eni mwamutupitsa mchomboyo mumutani? Zofunatu izo! Mukuvutitsa ana osalakwa, za zii! Ndikufuna bambo anga Anatchereza, Ndine Efrida Lungu kwa Kayembe, T/A Wimbe ku Kasungu. Ndimangomva kuti bamboo anga ndi a Lungu, Achitumbuka ndipo akuti alipo. Ine ndimafunitsitsa nditawaona. Akuti ankaphunzitsa pa Chamama School ndi pa Chimbowe. Akuti adandisiya ndili ndi zaka ziwiri koma pano ndili ndi zaka 19 ndipo ndili Form 4. Amene angawadziwe chonde tilumikizane pa 0999 810 665/0885 831 843/0997 249 347 . Ambuye akudalitseni. +Ofuna banja Ndine mayi wa zaka 26 ndikufuna mwamuna wa zaka 28. Ndili ndi mwana mmodzi. Mwamunayo akhale Mkatolika. Wondifuna aimbe pa 0884 484 963. +Nganga yochotsetsa mimba ithawa ku Mchinji Kwa Brenda Tadi, singanga Nasikiti udali ulalo wochotsera pathupi kufuna kuzemba uchembere omwe tate wake sakudziwika koma mapeto ake watsikira kuli chete. +Singangayo atazindikira kuti mankhwalawo agwira ntchito molakwika adasamuka mwachinsinsi ndipo mpaka pano anthu a mmudzimo ndi apolisi sakudziwa komwe adalowera. +Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Wojambula watu akuona ngati zidali choncho patsikulo Msungwanayu yemwe adali ndi zaka 20 adazindikira kuti ali ndi pathupi pa miyezi itatu ali kale ndi mwana wina wa chaka chimodzio ndipo sadali pabanja. +Mneneri wa polisi ya pa Mchinji Moses Nyirenda adatsimikiza za imfa ya Tadi ndipo adati wachinansi wake, Chifundo White, adauza apolisiwo kuti Tadi adakwatiwapo koma banja lidatha ndipo amangokhala pankhomo pamakolo ake. +White adati pa 11 October, 2015 Tadi atazindikira za mimbayo adapita kwa singanga Nasikiti yemwe adamupatsa mankhwala azitsamba nkumuuza kuti akamwe kuti mimbayo ikachoke koma zinthu zidatembenuka. +Atamwa mankhwalawo, pa 12 [October 2015] adayamba kudandaula mmimba momwe amagudubuka namo nkumabuula ngati mwana. Titamufunsa adaulula kuti adakatenga mankhwala ochotsera mimba kwa singanga Nasikiti, adatero White. +Iye adati singangayo adali wodziwika kuderalo koma sadamvekeko mbiri yopereka mankhwala omwe zotsatira zake zidali zomvetsa chisoni ngati imfa ya mnasi wake, Tadi. +White adati Tadi adamwalira pa 13 October 2015 vuto la mmimbalo litafika posautsa kwambiri ndipo azitsamba ena atalephera kukonza zinthu. +Nyirenda adati za imfa ya msungwanayo zitamveka, anthu adali balalabalala kumusakasaka koma sadamupeze ndipo apolisi atafika kusakako kudapitirira komabe popanda chooneka. +Iye adati singangayo akadzapezeka adzazengedwa mlandu wopereka mankhwala oipa kwa munthu komanso kuchotsa pathupi zomwe zimatsutsana ndi malamulo a dziko lino. +Tadi amachokera mmudzi mwa Nkhumba T/A Mavwere mboma la Mchinji. +kuderalo koma sadamvekeko mbiri yopereka mankhwala omwe zotsatira zake zidali zomvetsa chisoni ngati imfa ya mnasi wake, Tadi. +White adati Tadi adamwalira pa 13 October 2015 vuto la mmimbalo litafika posautsa kwambiri ndipo azitsamba ena atalephera kukonza zinthu. +Nyirenda adati za imfa ya msungwanayo zitamveka, anthu adali balalabalala kumusakasaka koma sadamupeze ndipo apolisi atafika kusakako kudapitirira komabe popanda chooneka. +Iye adati singangayo akadzapezeka adzazengedwa mlandu wopereka mankhwala oipa kwa munthu komanso kuchotsa pathupi zomwe zimatsutsana ndi malamulo a dziko lino. +Tadi amachokera mmudzi mwa Nkhumba T/A Mavwere mboma la Mchinji. +Adutse ndani mu Standard Bank? Ndime ya kotafainolo mu Standard Bank Cup yafika podetsa nkhawa pamene matimu anayi akuyenera kutsanzikana ndi chikhochi sabata ino. +Pamene timalemba nkhaniyi dzulo nkuti matimu a Civo ndi Dedza Young Soccer akuswana pa Civo Stadium. Dedza itatulutsa Kamuzu Barracks kudzera mmapenote ulendo wapitawo, dzulo imayenera kuona ngati ulendo ukhale wopitirira kapena kuthera panjira. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Lero ndiye ulipo wankhodzo za pusi pa Kamuzu Stadium pamene Red Lions ithambitsane ndi Be Forward Wanderers. +Wanderers idatulutsa Mafco kudzeranso mmapenote. Lero kodi Wanderers ichita zakupsa? Anthu ambiri ali ndi chikaiko malinga ndi kugonja motsatizana kwa Wanderers muligi ya TNM, koma kochi Elijah Kananji akuti awa ndi masewero osiyana ndipo akuona timu yake ikuphulapo kanthu lero. +Anyamata akungofunika kuwalimbitsa mtima, koma ndilibe chikaiko malinga ndi momwe akumenyera kuti masewero ndi Red Lions titha kusangalala, adatero Kananji. +Nayo Red Lions ikukumana ndi Wanderers itakumana ndi masautso pamene adagonja ndi Big Bullets 4-2 mligi. Koma Collings Nkuna akuti akubwera pa Kamuzu kuchokera ku Zomba ndi cholinga chofuna kupambana. +Ija idali ligi, apa tikukamba za chikho. Tikuyembekeza kuti tichita bwino mmasewero amenewa, adatero Nkuna. +Mpira wina lero ali pakati pa Silver Strikers ndi Blue Eagles pa Silver Stadium. Matimu onsewa zawayendera kumathero a sabata imeneyi muligi, Silver itapuntha Dedza 2-1 pamene Eagles idawalira Civo 4-1. +Silver, kukhala timu yomwe ikusunga chikhochi, sidagonjepo mligi chibwerereni Young Chimodzi ngati kochi. +Mawa ndiye kukhale fumbi ku Civo pamene Moyale Barracks ikhale ikusambitsana ndi Bullets. Bullets ikungochoka kosemphana ndi chikho cha Carlsberg chomwe idachisiya mmanja mwa Wanderers. +Wobwerera lili pululu amwaliranso ku zomba ZImene zachitika mmudzi mwa Makoloni kwa T/A Mwambo ku Zomba masiku apitawa nzoda mutu. Mayi wa zaka 28 amene adabwerera kumanda sabata ziwiri zapitazo bokosi la maliro lomwe adagoneka mtembo wake litayamba kunjenjemera, wamwaliranso atangokhala kwa masiku anayi. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Mfumu ya mmudzimo komanso woyandikana nyumba atsimikizira Msangulutso Lachiwiri lapitali za malodzawa ndipo ati anthu mmudziwo akuganiza kuti zachitikazi nzamasalamusi. +Wojambula wathu kufanizira ndi mmene zidakhalira tsiku limene Tamara Faliji adauka kwa akufa Patrick Matemba, yemwe adaona zododometsazi zikuchitika, adauza Msangulutso kuti Tamara Faliji adagwa kunyumba kwake masana a pa 11 August. +Sitikudziwa chomwe chidachitika koma adangogwa. Tidamutengera kuchipatala cha Makwapala Health Centre komwe adatiuza kuti wamwalira, adatero Matemba. +Monica Mbewe, namwino wa pachipatalachi yemwe adatsimikiza za imfayo poyamba, adauza Msangulutso kuti zomwe wodwalayo amaonetsa zidasonyeza kuti wamwalira. +Adafika ali ndi moyo ndipo ndidayamba kumupatsa thandizo. Patatha mphindi 30 ndidaitanidwanso ndi amene amamuyanganirawo kuti ndikaone zomwe akuchita. Panthawiyo amaonetsa zizindikiro zoti wawalira. +Pamtima sipamagunda, thupi lidangolobdoka, diripi ya madzi ndi mankhwala idasiya kuyenda. Apa zidasonyeza kuti wamwalira moti ndineyo ndidalembera kuti wamwalira, adatero namwinoyu. +Nyakwawa Makoloni potsimikiza za nkhaniyi, idati itamva za malirowo, idalamula anthu kuti ayambe kukonzekera zoika maliro mawa lake. +Mawa lake adzukulu adakumba manda ndipo anthu a mmudzimu adakhoma bokosi. Mwambo wa maliro utatha tidanyamula zovuta, ulendo kumanda, idatero mfumuyi. +Koma Makoloni adati anthu adadabwa kuona bokosi likugwedera atangofika kumanda. +Apa nkuti mwambo wakumandako utangoyamba kuti titsitsire bokosi mmanda ndipo ndidalamula kuti bokosilo litsekulidwe. +Titatsekula tidaona kuti wakufayo akutuluka thukuta komanso amadziwongolawongola, adatero Makoloni. +Iye adati mwambo udathera panjira ndipo adakwirira dzenje la mandalo nabwerera ndi woukayo kunyumba komwe kudaitanidwa ampingo wina wa Pentecost kuti amupempherere. +Pakulowa kwa tsikulo, akuti mayiyo adakwanitsa kudya phala koma movutikirabe. +Amangovumata, kuti ameze ndiye kudali kovuta, komabe adadya pangono, adatero Matemba. +Kulankhula ndiye adasiyiratu ndipo pamasiku onsewo amangodya phala. Pa 16 August adadzuka wolefuka ndipo adasiya kudya. Kenaka mpamene timamva kuti wamwaliranso. +Tidakhulupirira kuti ulendowu adamwaliradi chifukwa mkhwapa mudali mutazizira ndipo samatulukanso thukuta. Tidakaika maliro pa 17 August, adatero Makoloni. +Koma mfumuyi yati ikuganiza kuti zomwe zidachitikazo zidali zamasalamusi ndipo akukhulupirira kuti imfa ya mayiyo wina adaikapo dzanja. +Chilowereni ufumu zotere sindidazionepo. Ineyotu ndikuti ndidali pomwepo ndipo ndidadzionera zonsezi zikuchitika. Ndinadabwa nazo ndipo ndikukaika kuti zotere zingangochitika; alipo amene akukhudzidwa kuti mpaka mayiyu afe imfa yotere, idatsindika mfumuyi. +Akuti malirowo atangochitika, adzukulu ndi anthu ena adamenya gogo ake a womwalirayo pomuganizira kuti akukhudzidwa ndi imfa yachilendoyo. +Azula chamba, achiyatsa ku KK Nkhani zoti apolisi alanda kapena azula chamba ndi zina zokhudza mbewu yozunguzayi sizikukata mboma la Nkhotakota. +Lachiwiri sabata ino apolisi mbomalo, mogwirizana ndi asirikali oyanganira nkhalango ndi malo osungirako nyama zakutchire adazula chamba mmunda wamaekala atatu. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Izi zachitika apolisi pa 12 September ataotchanso matani 4.5 a chamba amene adalanda kwa njonda zina. +Aka nka chi 48 nkhani za mtunduwu kuchitika mbomalo chiyambireni January chaka chino, apolisi atero. +Mneneri wa polisi mbomalo, Williams Kaponda, adati munda womwe adazula chambachi uli pakati pa midzi ya Senior Chief Mwadzama ndi T/A Mwansambo. +Tidapeza chamba chochuluka mmundawu ndipo tidachizula ndi kuchiyatsa. Kufikira lero [Lachiwiri] palibe amene wanjatidwa pa nkhaniyi, koma apolisi tikufufuza kuti tipeze mwini mundawu, adatero Kaponda. +Izi sikuti timapanga tokha, tidali ndi mboni zina monga akuluakulu a bwalo la milandu, khonsolo ya Nkhotakota, achipembedzo, atolankhani, a ku Parks and Wildlife Game Reserve ndi ena. +Malinga ndi Kaponda, minda ina ya chamba yapezeka mmidzi ya Mwalawamphasa ndi Kanjedza mboma lomweli. Monga mwa mwambi woti moto umapita kumene kwatsala tchire, mmeneri wa polisiyu akuti mindayi nayonso aibutsa posachedwapa. +Nkhanizi zikudza pamene pali mtsutso ngati kuli koyenera kuti dziko lino livomereze chamba kuti anthu azilima komanso kugulitsa. Mdziko muno chamba ncholetseddwa kkaamba koti chimazunguza ubongo. +Boma la Nkhotakota limatchuka kwambiri ndi nkhani za chamba, chomwe anthu amalima mobisa mminda ya chinangwa, nzimbe ndi chimanga. +Aoloka yorodani pamtsinje wa ruo Sukulu adalekera sitandade 4, kuwerenga nkomuvuta, koma kuwerengera ndalama kwa iye si nkhani. Ngakhale sukulu sadapite nayo patali, ntchito zake zikuthandiza anthu oposa 15 000 kwa T/A Mlolo mboma la Nsanje. +Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Ndi manja ake, mnyamatayu wamanga mlatho wa mamita 100 pamtsinje wa Ruo womwe anthu ambiri tsopano akuolokerapo tsiku ndi tsiku. +Mavuto atha: Ana asukulu, abizinesi ndi opita kuchipatala tsopano akutha kuoloka Ruo Nzoonadi, aja adati wopusa adaimba ngoma, ochenjera navina sadaname, tikatengera nkhani ya Laitoni Anoki, wa zaka 28, yemwe amachokera mmudzi mwa Khasu. +Ngati ena poyamba ankamutenga ngati wopanda phindu kaamba koti sukulu adatulukira pawindo, lero wasanduka momboli wawo. Ngakhale mafumu mderali akuvomereza kuti Anoki ndi ngwazi ya anthu kumeneko. +Njinga zamoto, zakapalasa komanso matumba a chimanga ndi zigubu za mafuta zikuoloka pamenepa popanda vuto. +Zonse zidayamba ndi madzi osefukira amene adavuta chaka chino. Chifukwa chosefukira mtsinje wa Ruo udaiwala khwawa nkuphotchola. Midzi yambiri idakokoloka, anthu makumimakuni adafa pangoziyo, osanena za ziweto ndi kukokoloka kwa minda. +Mtsinjewu udachititsa kuti anthu azilephera kupita kuchipatala ku Makhanga Health Centre, kusukulu yasekondale ya Makhanga, komanso kumsika wa Admarc mderali. Mtsinjewo wachitanso malire ndi dziko la Mozambique komwe anthuwa amapitako kukasuma chimanga kutsatira njala yomwe yagwa mbomali komanso ndiko kukuchokera mafuta ophikira. +Poyamba, anthuwa ankangoyenda osaoloka mtsinje chifukwa padalibe mtsinje. Ankaoloka Ruo pokhapo ngati akupita ku Mozambique. +Anthu a derali, kudzera mwa mafumu awo, akhala akupempha mabungwe komanso boma kudzera mwa phungu wawo Esther Mcheka Chilenje kuti awamangire mlatho pa Ruo koma kuli chuu. +Ngoziyi itangochitika, phungu wathu adabwera kudzationa ndipo adatitsimikizira kuti atimangira mlatho poona kuti sitingathenso kupita kuchipatala ndi madera ena. Koma mpaka lero sitikudziwa kuti lonjezoli litheka liti, adatero gulupu Manyowa. +Adadza ndi nzeru zomanga mlatho: Anoki Manyowa akuti anthu pafupifupi 15 000 ndiwo akhudzidwa mwa magulupu 13 onse a mwa T/A Mlolo. +Ataona kufunika kwa mlatho pamtsinjewu Anoki, ngati wamisala, adayamba kudula mitengo nayamba kukhoma mlathowo. +Pocheza ndi Msangulutso, mnyamatayu akuti adayamba ntchito yomanga mlathowu mvula ili pafupi kusiya, apo nkuti madzi akulekeza mkhosi. +Poona kuti ntchito indikulira ndidakopa anyamata ena kuti tithandizane. Tidalipo 8. Tidadula mitengo ndipo ina ndimachita kugula. Ndidakagula misomali, ina anthu adangotipatsa koma ina ndidachita kukongola pamtengo wa K40 000. +Zida zitakwana, tidayamba kukhoma mitengo pamadzipa. Timasongola kaye mitengoyo ndi kukhoma ndi hamala. Ntchito idalipo chifukwa madzi nkuti ali ambiri moti mwina amandilekeza mkhosi, adatero Anoki. +Pakutha pa miyezi itatu, mlatho wotalika ndi mamita 100 nkuti utatha ndipo anthu adayamba kuolokerapo. +Ngakhale tidamaliza komabe tsiku lililonse timaugwiragwira chifukwa pena umapeza msomali wazuka kapena mtego wachoka chifukwa pamadutsa anthu ambiri, adatero. +Lero Anoki wayamba kudyerera thukuta lake pamlathowu. +Munthu mmodzi amalipira K100 kupita ndi kubwera. Njinga yamoto timalipitsa K200, thumba lolemera ndi makilogalamu 50 timalipitsa K100, koma opita kuchipatala sitimawalipiritsa. +Patsiku Anoki akuti amapanga ndalama yosachepera K20 000. Sungadabwe kumuona mnyamatayu lero akutuluka mnyumba yanjerwa zootcha komanso yamalata, ndipo wagula mbuzi zingapo, kumunda waikako aganyu. +Kupatula apo, Anoki walemba ntchito anyamata asanu kuti azithandizira pamlathowo. +Anthu amaoloka ndi usiku womwe. Komanso pakufunika anthu olondera ndiye pali anyamata asanu amene akuthandiza. Ena amathandizira kuolotsa njinga. Patsiku ndikumawalipira K1 500 aliyense, adatero Anoki. +Anyamata amene adamanga nawo mlathowu akulandiranso zawo. Chomwe tapanga nkuti tizigawana sabata yolandira ndalamazi. Sabata ino ndilandira ndineyo, ndiye kuti wina alandira sabata yamawa. +Mmene tikuteremu ndiye kuti ndalama yokonzetsera mlathowu imakhalanso tasunga. Mukuona anthu akubweretsa mitengo, amenewa tikufuna tiwagule kuti zida zikhale zokwanira, adatero Anoki, uku akusintha ndalama zopatsa kasitomala. +Mphindi 20 zomwe tidakhala pamlathowo, onyamula zigubu za mafuta ndi matumba a chimanga kuchokera mdziko la Mozambique, opita kuchipatala komanso ophunzira ndi alimi ndiwo amaoloka mowirikiza. +Lero dzina la Anoki silisowanso mmudzimo. Gulupu Manyowa akuti alibe naye mawu mnyamatayu. +Mtsinje umenewu ndi waukulu, anthu 9 a mmudzi mwanga adapita akuoloka mtsinjewu. Lero tikutha kumaoloka mwaufulu, zomwe sitidaziganize chifukwa maso anthu adali kuboma. Izi zidatipatsa chimwemwe. +Pano tikumapita kumsika, kusekondale, ku Mozambique komanso ku Admarc mopanda vuto. Simungapite ku Bangula kuchokera kuno osadutsa pamlathowu, adatero Manyowa amene akuti masiku ena samalipitsidwa. +Mkulu wina amene ankapita kuchipatala ndi bambo ake adati mlathowu wawathandiza kopambana. +Mkuluyu, Gift Filipo, wa mmudzi mwa James kwa Gulupu Mchacha, akuti pachipanda mlathowu sakadapita ndi bambo ake kuchipatalako. +Flames inyamuka mawa Timu ya Flames ikunyamuka mawa mdziko muno ulendo ku Tanzania kukaswana ndi timuyi masewero amene alipo Lachitatu pa 7 October. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Iyi ndi ndime yachipulula mumpikisano wa Fifa 2018 World Cup ndipo masewero achibwereza ali Loweruka likudzali pa Kamuzu Stadium. +Malinga ndi mlembi wa Fam Sugzo Nyirenda, osewera akumana cha mma 6:00 madzulo ano kuchoka kosewerera makalabu awo. +Timu ikanyamukira ku Lilongwe nthawi ikamati 7:30 mmawa. Masewerowa akachitikira pabwalo la Benjamin Mkapa ndipo adzayamba 3:00 masana nthawi ya ku Malawi kuno. +Mtawali adatenga osewera monga Simplex Nthala, Bighton Munthali, Stanley Sanudi, John Lanjesi, Yamikani Fodya, Miracle Gabeya, Pilirani Zonda, Limbikani Mzava, Isaac Kaliati, Chimango Kaira, Robert Ngambi, Micium Mhone, John CJ Banda, Levison Maganizo, Gerald Phiri Jnr, Dalitso Sailesi, Manase Chiyese, Robin Ngalande, Chawanangwa Kaonga ndi Frank Gabadinho Mhango. +Eid al Adha: Chikondwerero chopereka nsembe Chaka ndi chaka a chipembedzo cha Chisilamu amakhala akuzinga ziweto nthawi ina. Pa mwambowu, Asilamu amakhala akutsatira zomwe Mulungu adalamula Abraham zaka zammbuyo. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Sheikh Malekano Rajab ndipo adakambirana motere: Poyamba, ndikudziweni. +Chisale watuluka nkumangidwanso Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Ndine Sheikh Malekano Rajab ndimatumikila pamzikiti wa pamsika wa Area 22 ku Lilongwe. +Kodi chaka ndi chaka Asilamu amakhala ndi mwambo wopha ziweto talongosolani kuti zimakhala bwanji? Mwambo umene uja timakhala tikukumbukira zomwe Mulungu adauza Abrahamu kalelo nthawi yomwe adavomera kupereka mwana wake Ishmael nsembe. Akuti azipereka mwanayo nsembe, Mulungu adatumiza nkhosa ndipo mwanayo adapulumuka. Mulungu adalamula Abrahamu kuti chaka chilichonse Asilamu azikhala ndi mwambo umenewu ngati chikumbutso komanso kulemekeza Mulungu. +Mwambowu umachitika liti? Umachitika tsiku la khumi (10) la mwezi wa chisanu ndi chinayi mkalendala ya Chisilamu. Pakafika pa 1 mwezi umenewo msilamu aliyense amayenera kuyamba kusala kwa masiku 10 ndipo kusalako kumatha tsiku la nambala 10 lomwe kumakhala kuzinga ziweto kapena chikwenderero cha Eid al Adha. Chimachitika nchiyani pa tsikuli? Msilamu amayenera kugula chiweto monga ngombe kapena mbuzi nkupha. Nyama yake nkugawa koma naye mwini wake amayenera kutengapo gawo osangogawa yonse ayi. Kupha nyamako kumatchedwanso Qrubani. +Chiweto chake chimayenera kukhala chotani? Chiweto chikhoza kukhala chilichonse koma chikhale chopanda chilema kapena choti chidakokako ngolo kapena chidalimako. Chikhale chiweto chalunga ndipo chopanda ngakhale chilonda pathupi lake komanso chathanzi. +China chimachitika nchiyani? Lisadafike tsikulo, Asilamu a ndalama zawo amapita ku Mecca. Ulendo wopita ku Mecca umatchedwanso kuti haji ndipo ndi imodzi mwa nsanamira za Chisilamu. Omwe alibe ndalama amakhala kumudzi koma nawonso amakhala akutsatira zoyenera kuchita kuti tsikulo lisadetsedwe. +Nanga wina akaphonyetsa monga kupha chiweto chodwala zimakhala bwanji? Pamenepo nsembe imeneyotu siyilandiridwa chifukwa ndiyodetsedwa ndipo ndiyosayenera kuperekedwa kwa Mulungu. Nthawi zonse munthu amayenera kukumbuka kuti iyi ndi nyengo yoyera yoyenera kuyeretsedwa. +Nanga aja amakhala akuimbawa amatinji? Amene aja sakhala akuimba nyimbo, amakhala akupemphera pemphero lomwe mngelo Gabriel ankanena akudzapereka nkhosa yomwe Abrahamu adasinthitsa ndi mwana wake yemwe adakonzeka kukamupereka nsembe. Pemphero lake limati Mulungu ndi wamkulu palibe ofanana naye ndipo iye ndiye tate basi. +Nanga ochepekedwa ndalama sizingatheke kugula nyama yophaipha nkugawa? Ayi sizingatheke pamafunika kuchita kupha ndithu. Kugula ndi kugawa yophaipha ndiye kuti sikhalanso idi koma sadaka. Komanso umayenera kupha tsiku lenilenilo kapena masiku atatu otsatira kupanda apo, imeneyonso ndi sadaka odati idi ayi. +Ndiye mwati zidayamba liti? Zidayamba kalekale nthawi ya Abrahamu pomwe Mulungu adamuuza kuti mwezi wa nambala 9, kuyambira pa 1 ndipo tsiku la nambala 10 kuzichitika mwambo oterewu. Kuchoka pa Abrahamu, aneneri onse omwe ankabwera kufikila pa Muhammad amatsatira zimenezi ndiye Asilamu onse amayenera kutsatira. +Panazale samakololapo! Flames yalepherana mphamvu ndi Swaziland 2-2 kusonyeza kuti mgulu L la mpikisano wolimbirana chiko cha Africa Cup of Nations (Afcon) Malawi ili panambala 3 ndi pointi imodzi mmasewero awiri itagonja pakhomo ndi Zimbabwe mmasewero oyamba mu June. +Kochi Ernest Mtawali akukhulupirira kuti Flames ichitabe bwino mu Afcon pamene yatsala ndi masewero anayi. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Kudabwitsa kwake nkoti iye akugwiritsa ntchito osewera amene ndi apanazale. Kodi a kochi, panazale amakololapo? Osewera mukugwiritsa ntchitowa sangatibweretsere zotsatira lero ndi lero. Ngakhale dziko la Malawi ndi la njala ndi kupambana, bwana Mtawali mungotilimbitsa mtima ponena kuti mumpikisanowu tituluka. +Mukadafuna zokolola bwezi mutatenga achina Esau Kanyenda kuti akathandize ntchito anawa kutsogoloko. Pamene Micium Mhone adavulala, ife timayembekeza kuti Robert Ngambi alowetsedwa. +Naye Gerald Phiri Jnr adaonetsa kuti akutopa chigawo chachiwiri chija zomwe zimafunika kuti Frank Banda agwire ntchito. Koma mudakhulupirira ana aja ndiye mukuganiza kuti tidakakololapo? Tikakhala ife aganyu ndiye sitidamvere nawo mpirawo. Pajatu mzipatala mulibe mankhwala ndiye Flames yanuyo ikatikweza BP tipita kuti? Kumbukirani malangizo a achipatala poonera Flames: Chonde onetsetsani kuti BP yanu mwayezetsa bwinobwino popewa kutifera. Gulani kabotolo ka Panado popewa mutu wachingalangala. Gulani thanzi ORS popewa mmimba mwa mpezepeze ndi mothulula. Ngati mukuonera usiku, onetsetsani kuti mwagula mankhwala ogonetsa. +Amayi pempheranitu ndalama ya ndiwo kwa amuna anu. Mwana asayandikire bambo ake gemu ikatha. Musayandikane ndi madzi otentha. Musayandikire zinthu zosweka. Musakhale pafupi ndi mbaulae. +Boma likukhazikitsa misika ya zakudimba Boma lili mkati momanga malo ogulitsira zokolola zakudimba ngati njira imodzi yochulukitsira phindu lomwe alimi amapeza pogulitsa zokolola zochokera mu ulimi wamthirira. +Ntchitoyi ndi gawo limodzi la ntchito yotukula ulimi wamthirira pokonzanso masikimu 11 mchigawo cha zaulimi cha Blantyre Agricultural Development Division (ADD). +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mkulu woyanganira ntchito yotukula zipangizo za ulimi wamthirira, Cosmos Luwanda wati misikayi, yomwe ilipo 6, imangidwa ku Neno ndi kuchigwa cha mtsinje wa Shire. +Iye wati ntchitoyi, yomwe ikugwirika ndi thandizo la ndalama zokwana 12 biliyoni kwacha kuchokera ku African Development Bank (ADB), imanga manthu wa misika mumzinda wa Lilongwe komwe kutakhale zipangizo zapamwamba zotha kusungira ndiwo zamasamba ndi zipatso kwanthawi yaitali. +Cholinga cha misikayi ndi kulumikiza alimi ndi ogula mosavuta, adatero Luwanda. +Mkulu woyanganira ntchito yomanga msika wa zokolola za kudimba wa Chikwawa, Khama Kammwamba, adati malowa adzakhala ndi malo osungira zokolola, malo otsukira zokolola, magetsi, madzi apampopi ndi zimbudzi zamakono. +Misikayi izidzagulitsa zokolola mwachipiku kwa amalonda ochokera kutali. Adindo oyendetsa masikimu ndi amene azidzayendetsa misika imeneyi, adatero Kammwamba. +Padakalipano ntchito yokonza masikimu amene ali mupolojeikiti imeneyi ili mkati ndipo masikimuwa akuyembekezeka kuyamba kugwira ntchito yawo usanafike mwezi wa June chaka chamawa. +Wofuna kuba alubino amusinthira mlandu Mkulu yemwe akuimbidwa mlandu wofuna kuba alubino ndi cholinga chomupha zidamuthina Lachiwiri lapitali kubwalo la milandu la majisitireti ku Mzuzu pomwe boma lamusinthira mlandu. +Tsopano Phillip Ngulube, wa zaka 21, akuyankha mlandu wofuna kupha munthu, womwe ndi waukulu kuposa wozembetsa munthu ndi cholinga chofuna kumupha. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Wa kulimandi: Ngulube (kumanzere) pambuyo pokaonekera kukhotiWa kulimandi: Ngulube (kumanzere) pambuyo pokaonekera kukhoti Ngati Ngulube angapezeke wolakwa pamlandu watsopanowu akhoza kukakhala kundende moyo wake wonse. +Ngakhale Ngulube adavomera mlandu woyambawu pa September 15 pomwe adakaonekera kubwaloli koyamba, mlandu watsopanowu waukana. +Ndikukana kuti ndinkafuna kumupha mtsikanayu. Zoona zake ndi zoti ndinkamufuna banja basi, iye adauza bwaloli. +Yankholi lidadzi-dzimutsa majisitireti Gladys Gondwe chifukwa woganiziridwayu ankangoyenera kunena ngati akuuvomera kapena kuukana mlanduwu. +Komabe woweruzayu adalemba kuti waukana poti woimira boma pamlanduwu ayenera kupereka umboni mwatsatanetsatane kuti cholinga cha woyankha mlanduwu chidali kupha chibwezi chakecho. +Wapolisi woimira boma pamlanduwu, Christopher Katani, adalonjeza kuti abweretsa mboni zisanu ndi ziwiri pamene bwaloli lidzakumanenso pa September 30. Zina mwa mbonizi ndi Mswahili yemwe akuti adatsatsidwa malonda a mwalubinoyo kuphatikizapo mtsikana mwini wakeyo. +Malinga ndi mneneri wa apolisi mchigawo cha kumpoto, Maurice Chapola, oimira boma pamlanduwu aganiza zosintha poyesayesa kuti ozunza maalubino azilandira zilango zokhwima pofuna kuthetsa mchitidwewu. +Bwalo la milanduli lidamva kuti Ngulube, yemwe amagwira ntchito ya uphunzitsi modzipereka pasukulu ya pulaimale ya Mongo, adafunsira mbeta mtsikana wachialubino, wa zaka 17, ndi cholinga chofuna kumuba kuti akamugulitse pamtengo wa K6 miliyoni. +Kupha ndi kugulitsa anthu achialubino, makamaka ana, wayamba kukula mdziko muno pamene boma la Tanzania laletsa usinganga mdzikomo womwe akuti wapangitsa kuti maalubino ambiri aphedwe ndi anthu ofuna zizimba. +Ku Tanzania ndi maiko ena a kuvuma kwa Africa ena amakhulupirira kuti ziwalo za munthu wachialubino ndi zizimba zopangira mankhwala ochulukitsira chuma ndi mwayi. +Chidwi pantchito ya uphunzitsi chizilala Bungwe la aphunzitsi mdziko muno la Teachers Union of Malawi (TUM) lati zomwe lachita boma pokhazikitsa mfundo yoti ofuna kuphunzira ntchito ya uphunzitsi mmakoleji a boma (Teachers Training CollegeTTC) ayambe kulipira zichititsa kuti ambiri asakhale ndi chidwi cholowa uphunzitsi. +Woyendetsa ntchito za bungweli, Charles Kumchenga, adanena izi pothirirapo ndemanga pa ganizo la boma loti ophunzira ntchito ya uphunzitsi mmakoleji 8 a boma azilipira ndalama zokwana K105 000 pachaka kuonjezera pa ndalama zomwe boma limapereka. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Pakalipano ngakhale mwana wapulayimale kumufunsa ntchito yomwe amafuna kudzagwira, ambiri satchula ya uphunzitsi chifukwa amaona okha mmene aphunzitsi akuvutikira, ndiye pano akuti munthu uzilipiranso ndalama zambirimbiri kuti ukhale mphunzitsiambiri chidwi sakhalanso nacho, adatero Kumchenga pouza Tamvani. +Kumchenga adati zinthu zambiri sizili bwino nkale mmakoleji a aphunzitsizi ndipo nthawi zonse boma limathamangira kuti ndalama ndizo zavuta likafunsidwa kukonza zina mwa zinthuzo. +Ndi zoonadi boma lati aphunzitsi azilipira kuti aphunzire ntchito koma nkhawa yathu ili pakuti kodi izi zisintha zinthu msukulu zophunzitsiramo aphunzitsizi? Pali zambiri zofunika kukonza monga malo ogona, chakudya ngakhalenso malo ophunziriramo, adatero Kumchenga. +Iye adati ndi zomvetsa chisoni kuti ntchito ya uphunzitsi imatengedwa ngati yotsalira kwambiri pomwe ndiyo gwero la ntchito ina iliyonse. +Kumchenga adatchulapo kusowa kwa nyumba zokhalamo aphunzitsi, kuchedwa kukwezedwa pantchito, malipiro ochepa, kuchedwa kwa malipiro ndi ndalama yolimbikitsira aphunzitsi akumidzi ngati ena mwa mavuto omwe amalowetsa pansi ntchito za maphunziro. +Koma poikira kumbuyo zomwe boma lachita, mlembi wamkulu muunduna wa zamaphunziro, Lonely Magreta, wati boma lidaganiza zoyambitsa kulipira mma TTC ndi msukulu zina pofuna kutukula ntchito za maphunziro. +Iye adati kudalira boma lokha sikungapindule kanthu chifukwa lili ndi zambiri zofunika kuchita ndiye kugawana udindo kungathandize kuti zinthu zisinthe msanga. +Cholinga chathu nchakuti ntchito za maphunziro zipite patsogolo. Mwa zina, tikufunitsitsa kuti zipangizo zophunzitsira ndi zophunzirira zizikhala zokwanira kuti wophunzira aliyense azikhala ndi buku lakelake panthawi yophunzira, adatero Magreta. +Iye adati wophunzira aliyense ku TTC azipereka K105 000 pachaka yomwe ikuyimirira K20 pa K100 iliyonse yomwe imafunika kusula mphunzitsi mmodzi pachaka, kutanthauza kuti boma limafunika ndalama zokwana K525 000 pa mphunzitsi mmodzi. +Kupatula kuyambitsa zolipira mma TTC, boma latinso aliyense wofuna kukachita maphunziro ku Domasi komwe aphunzitsi amakaonjezera maphunziro awo, azilipira yekha. Wadipuloma azilipira K180 000 ndipo wofuna digiri ndi K280 000 pachaka Kusinthaku kwakhudzanso sukulu za sekondale komwe fizi yakwera kufika pa K12 000 ku MCDE; K10 000 kusekondale yoyendera; msekondale zothandizidwa ndi boma K75 000. Kuyunivesite komwe akuti aliyense azilipira payekha, fizi ndi K275 000 pachaka, pomwe mmbuyomu osankhidwira kumakoleji a University of Malawi ankalipira K55 000 yokha pachaka, pamene ofuna kudzilipilira ankalipira K275 000. +Kuphatikiza apa, boma lati lasiya kupereka alawansi yomwe ophunzira ankalandira kuti iziwathandiza pogulira zipangizo monga mabulu ndi zowathandiza pamaphunziro awo. +Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe oyanganira zamaphunziro mdziko muno la Civil Society Education Coalition (Csec), Benedicto Kondowe, waati ganizo la bomali lili bwino, koma labwera molakwika. +Pocheza ndi Tamvani, Lachiwiri lapitali, Kondowe adati zomwe lachita boma polengeza kusinthaku modzidzimutsa zichititsa kuti anthu ambiri omwe adali ndi chilakolako cha sukulu alephere kuchita maphunziro awo chifukwa sadakonzekere mokwanira. +Mwachitsanzo, mukatengera ndalama zomwe amalandira aphunzitsi, [wa PT4 wongoyamba kumene ntchito amalandira K54] ndi angati angakwanitse kusunga ndalama yokalipira ku Domasi kuti akaonjezere maphunziro? Izi zikutanthauza kuti aphunzitsi ambiri aimira pomwe alipo basi, ndiye maphunziro sangatukuke choncho,adatero Kondowe. +Iye adati boma limafunikira kukonza ndondomekoyi ndi kulengeza panthawi yabwino kuti anthu akonzekere, osati kungowadzidzimutsa, ayi. +Mayi wamalonda avulazidwa ku bt Titha Masamba, wa zaka 31, akumva ululu wadzaoneni. Kuti ayende akuyenera agwirire ndodo; sangagone chafufumimba koma chammbali kapena chagada; moyo wamtendere watha. +Akuti adamuphera tsogolo lake: Masamba kumva ululu kunyumba kwake Akuti izitu zili chonchi chifukwa cha bala lomwe lili pabondo lake la kumanja lomwe lidasokedwa kuchipatala pambuyo pokhapidwa ndi chikwanje. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ulendo wa mayiyu wokagulitsa mandasi pa 7 July ndi womwe udabweretsa mavutowa pomwe anthu ena, omwe akuwaganizira kuti ogwira ntchito kukhonsolo ya mzinda wa Blantyre (city rangers) amene adamuchita chiwembu pomulanda malonda ake komanso kumuvulaza ndi chikwanje. +Masamba akuti atangomwalira amuna ake mu 2007, iye adayamba geni yogulitsa mandasi kuti azisamalira banja lake la ana awiri. Malo amene amagulitsira malonda akewo akuti ndi ku Cold Storage pafupi ndi Kamuzu Stadium mumzindawu. +Monga mwa nthawi zonse, patsiku la ngozilo, adauyatsa ulendo wokapha makwacha. Pafupi ndi Cold Storage pali njanje ndiye ndidaika malonda anga chapafupi ndi msewu womwe umadutsa pamwamba pa njajeyo kuti ndikataye madzi ndisadalowere ku Cold Storage, adatero Masamba. +Pamene ndimati ndikatenge malondawo, ndidangoona galimoto ya City, yoyera ndipo mmbalimu idali ya sefa. Idadzaima pafupi ndi pomwe padali mandasiwo ndipo adali mgalimotomo adatsika natenga beseni la mandasilo. Ena adandigwira ndipo ndidawauza kuti angotenga mandasiwo asalimbane nane koma zidakanika. +Mayiyu, yemwe akukhala ku Makhetha mumzindawu, akuti anthuwo adamubudulira malondawo ndipo mosakhalitsa zodabwitsa zidamuchitikira. +Mmodzi adatulutsa chikwanje ndipo adandikhapa nacho pabondopa. Kaamba ka ululu kuchokera apo sindikumbukanso chomwe chidachitika ndipo ndidangozindikira ndili pabedi kuchipatala ku Queens cha mma 4 koloko madzulo, adatero. +Iye akuti adazindikiranso kuti K4 500 yomwe adamanga pansalu yake palibe. +Idali ndalama yomwe ndimati ndiwatumizire agogo anga ku Dedza. Agogowa amadaliranso ine akafuna thandizo, adatero iye. +Chichitikireni cha izi, mayiyu akungobuula ndi ululu kunyumba kwake. Geni sangachitenso, moyo tsopano wasanduka wovuta. +Mneneri wa khonsolo ya Blantyre Anthony Kasunda akuti wangomva za nkhaniyi koma akufufuza kaye ngatidi adali antchito awo amene adachitira chipongwe mayiyu. +Ndikudabwa chifuma malo amene mayiwa akukamba ife sitifikako. Ndiye zikundidabwitsa kuti zatheka bwanji kuti mayiwa avulazidwe ndi anthu amene akuti ndi akhonsolo ya Blantyre, adatero Kasunda, amene akuganiza kuti mwina angakhale anthu ena omwe achita izi. +Pamene Kasunda akufufuza, moyo wa Masamba uli pachiswe chifukwa ana ake akudalira iye kuti asake chakudya cha tsiku ndi tsiku komanso zofunikira kusukulu. +Andiphera tsogolo. Tikadya ndiye kuti ndachita geni. Nawo mpamba udathera kuchipatala. Chochita chikundisowa, adalira mayiyu pocheza naye kunyumba kwake. +Pepani Ngonamo, Chirwa Kudali ntchito ku FAM pamene amafuna kochi wa timu ya fuko ya Flames. Eddie Ngonamo, Nsanzurwimo Ramadhan, Ernest Mtawali ndi Gilbert Chirwa ndiwo adalembera ndipo a FAM atenga Mtawali ndi Ramadhan ngati kochi ndi wachiwiri wake. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Aganyu alankhula zambiri pa kutengedwa kwa akamunawa, komanso kuikapo maganizo awo potaidwa kwa Ngonamo ndi Chirwa. +Lero tikubweretsa zomwe aganyu akhala akulankhula pa za ganizo la FAM. Pamene ena akuti ganizo la FAM lilibwino, ena akuti zalakwika. +Amwene pamenepaja pakufunika Ngonamo. Mukudziwa kuti dala aja ali ndi Preparatory Certificate for A licence, akuphunzitsanso zamasewero ku Karibu Academy. A FAM adakonza kale zimenezo. +Mukudziwanso kuti dala aja adachita maphunziro limodzi ndi Jos Mourinho, komanso akhala akuphunzitsa mmaiko akunja. Basi dala aja asalemberenso ntchito imeneyi, chifukwa zikuoneka kuti samawafuna. Koma kuwasiya a Chirwa aja ndiye sadalakwe mukudziwanso kuti adaithawa Bullets, wina adatero. +Mkulu winanso adaperekapo maganizo ake. Zili bwino apapa, Ngonamo adalephera atapatsidwa mwayi ku Flames mu 2013. Flames idapambana gemu imodzi tikusewera ndi Namibia kwawo koma patsikulonso iyeyo panalibe. Namibia itabwera kuno tidalephera kuichinya. Amuchita bwino. +Komanso ndidamuona Ngonamo akukhazikitsa malamulo okhwima ukafuna kujambula Flames ku training, iye amati tizimupempha chifukwa bwana ndiyeyo. Inuyo mudazionapo kutiko zimenezi? Ngati mukuti akuphunzitsa ku Karibu ndiye kuti amaphunzitsa ana, ndiye mukufuna ayambe kuphunzitsa Flames mpakana? Imeneyo ndiyo ntchito ya pa Malawi. +A maufulu ayamikira MCP Akatswiri andale kudzanso mabungwe oimira ufulu wa anthu mdziko muno ayamikila chipani chachikulu chotsutsa boma cha Malawi Congress Party (MCP) powonetsa chitsanzo chabwino kwambiri potsata ndale za demokalase posankha anthu mmaudindo kupyolera mnjira yovomelezeka ya chisankho. +Chakwera (wachiwiri kuchokera ku manja) limodzi ndi mkazi wake Monica komanso akuluakulu ena kumsonkhanowo Mmiyezi iwiri yotsana ya July kudzanso August chaka chino, MCP yachititsa zisankho mu zigawo za kumwera ndi pakati. Ndipo mmenemo chaika anthu atsopano mmipando yosiyasiyana oyendetsa chipanichi mzigawozo. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Katswiri wa ndale ku sukulu ya ukachenjede ya University of Malawi chigawo cha Chancellor College a Mustapha Husseni, ati zomwe ikuchita MCP ndiye zoyenera komanso zofunika kwambiri pa ulamuliro wa demokalase mchipani. +Chipanichi mpofunika kuchiyamikira pazomwe chikuchitazi. Chikuchita ndale zololerana za-intraparty democracy, ndipo ife tingoti asaleke zimenezi chifukwa kumeneku ndiye kulimbitsa chipani mnjira yoyenera, atero a Husseni. +Malinga ndi mneneli wa MCP a Jessie Kabwira, chipanichi chichititsanso chisankho chonga chomwechi ku chigawo cha kumpoto. Iwo ati akuchita zimenezi kuti chipanichi chikhale cholimba, ndicholinga chakuti pomadzafika nthawi ya chisankho chachikuru chosankha prezidenti wadziko, aphungu, kudzanso makhansala mu 2019, chidzakhale cha mphamvu kwambiri mmadera onse adziko lino. +Mkulu wa Centre for the Deveopment of People (Cedep) , a Gift Trapence, sadabise mau kukhosi ponena kuti zimenezi sizachilendo ai, kaamba kakuti ndikofunikiradi kutero, maka poyanganila kuti eni ake a zipani za ndale ndi anthu wamba omwe ndiwochuruka. +Zotsatira zake nzakuti zinthu zikamayenda motero, anthu ambiri amakhala nacho chikhulupiliro chipani choterocho. Iwo amadziwa kuti pakutero icho chikutsatsa njira zabwino za democracy. Ndiponso izi sizifunika mchipani mokhamo ai, komanso ngakhale dziko lonse, adatero a Trapence. +Nawonso a Timothy Mtambo, a Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR), potsilira ndemanga afotokoza kuti MCP yawonetsa kukhwima nzeru mu ndale za demokalase poika anthu mmaudindo mchipanichi kudzera mnjira yovomelezeka yachisankho. +Zoonadi iyi ndi njira yabwino kwambiri, kusiyana ndikungoloza ndi chala kapena kumangosankhana ndi pakamwa pokha. Kuwonjezera pamenepa, ife tikupempha kuti zisathere pa maudindo angonoangono okhawa ai, komanso ngakhale wa pulezident ndi ena otere, zidzikhalanso chimodzimodzi. Pamenepa sitikunena MCP yokha ai, komanso zipani zonse za ndale mdziko muno, atero a Mtambo. +A Mtambo anatinso ndizodabwitsa kuti MCP yomwe inkakanitsitsa kubweretsa ndale za demokalse mu ulamuliro wake wa chipani chimodzi, lero lino ikuposa zipani zina, pokhala patsogolo kuwonetsa chitsanzo chabwino pa ndale za zipani zambiri mdziko muno. +A Mtambo anadzudzulanso mchitidwe omwe akuti zikuchita zipani zina mdziko muno, posankha mwana kaya mchimwene wake wa pulezident wa chipanicho kukhala mulowa malo, pomwe mtsogoleriyo akutula pansi udindo. +Ngakhale kuti mdziko muno muli ufulu wakuti wina aliyense akhoza kupikisana nawo pa udindo wina uliwonse, komabe, mchitidwe okhala ngati waufumu, osiilana udindo muzipani za ndale ukukhumudwitsa anthu, komanso kuwopseza chitetezo cha ndale za democray. +Zoterezi sizabwino nkamodzi komwe. Ndipo zitheretu. Apatu sitikunena muchipani cha ndale chokha ai, komanso ngakhale dziko lonse la Malawi. Tisawumilize anthu kuchita zomwe mwina iwo sakufuna. Alekeni otsatila chipani asankhe okha munthu yemwe akumufuna kuwatsogolera mchipanimo. Ndiye tikawonetsetsa, komanso kunena mwa chilungamo poyelekeza ndi zipani zina, zimenezo sitinaziwone pakali pano mu MCP. Pachifukwachi ndithu tikuwayamikira komanso kuwalimbikitsa kuti zimenezi apitilize, adatero Mtambo. +anatchezera Akuti tibwererane Anatchereza, Ndinali pambanja ndi mwamuna wa ku Nsanje ndipo ndili naye mwana mmodzi. Koma ndikati tiyeni tikaone kwanu amangoti tidzapitabe chikhalireni palibe ndi tsiku ndi limodzi lomwe abale ake anabwerapo pakhomo pathu ndiponso banja lathu ndi losagwirizira chinkhoswe. Kumudzi kwathu mwanuna wangayu amakananso kukaonako. Panopa tinasiyana chifukwa samagona mnyumba. Mowa samwa komanso fodya sasuta. Ndiye panopa akukakamira kuti tibwererane, apo bii ndimupatse mwana wake, koma ineyo ndikukana. Gogo, ndithandizeni. Nditani pamenepa? Mwati mudali pabanja, koma banja lanu padalibe chinkhoswe? Ndiye lidaali banja lotani lodziwa awiri nokhanu? Apa mukuchita kudabwa kuti a kwawo kwa mwamuna wanu sadabwerepo pakhomo panu ngakhale tsiku limodziakadabwerapo bwanji ngati akukudziwani? Munasiyana koma pano mwati akukakamira kuti mubwererane, pachifukwa chiti? Mwachidule, ndinene kuti mmphechepeche mwa njovu sapita kawiri. Kubwererana ndi mwamuna wotere kuli ngati galu kubwerera kumasanzi akepalibe chanzeru. Koma ngati watsimikiza kuti amakukonda ndipo nawenso umamukondabe, ulendo uno muyesetse kuti akwawo ndi akwanu akumane ndi kukambirana kuti pakhale dongosolo lenileni, chinkhoswe kenaka ukwati wovomerezeka ndi mbali zonsezonse. Pokhapo ndiye kuti mutha kumanga banja, osati zachibwana zimene mudachita kupatsana mwana kenaka wina aziti tibwererane apo bii undipatse mwana wanga. Banja si masanje, chonde! Zikomo, Natchereza Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Akuthawathawa Anatchereza, Mwezi wa April 2011 ndinapeza mwamuna ndipo sindinagonane naye kufikira 6 July 2012 pamene tinakaonekera kwa makolo a tonse. Tsiku limneli andiuza kuti tigonane koma ndinawauza kuti tikayezetse kaye HIV koma adakana ponena kuti iwo ndi blood donor choncho ndisawakaikire ndipo zinatheka. Titasiyana tsiku limenelo adandiuza kuti tikadziwe komwe amagwira ntchito ku Zomba. Nditapita andiuza kuti ndisabwererenso tiyambiretu banja koma ndinakana ndipo ndidabwerera. Patapita masiku adabwera ndi amalume awo kudzafunsira mbeta ndipo zinatheka. Pambuyo pake tidayamba banja ndipo posakhalitsa ndidaima. Mwanunayu adandiuza kuti mmamawa azidya phala ndipo nsima izikhala ya mgaiwa. Chodabwitsa chinali choti phala likafika patebulo limasintha mtundu kukhala lobiriwira (green) koma kuwafunsa samandiyankha zomveka. Nditalimbikira anandionetsa mabotolo awiri momwe munali zinthu za ufa za green koma anakana kundiuza ntchito yake, ati sizimandikhudza. Tsiku lina ananditenga kuti tikayezetse magazi koma titafika kumneko anandiyeza ndekha ati iwo adyezetsa kale. Anandipeza ndi kachilombo ka HIV. Kuyambira tsiku lomwelo anandiuza kuti banja latha ndizipita kwathu. Ndinakatula nkhaniyi kwa amalume awo koma palibe chikuchitika. Nditani? M Zikomo M, Sindidziwa kuti kachilombo ka HIV mudatatenga bwanji, koma sindikukaika kuti mwamuna wanuyo ndi amene adakupatsirani kachilomboko ndipo zikuonetseratu kuti amachita izi uku akudziwa kuti ali ndi HIV. Ndatero chifukwa cha zochita zakeakuonekeratu kuti alibe chilungamo mzochitika zake. Nanga timabotolo ta mankhwala obiriwira amathira mphalato ntachiyani? Nanga amakana kukayezetsa chifukwa ninji? Pano inu mwapezeka ndi HIV akuti banja latha, zoona? Ndithu, ngati iyeyo adali walungalunga, akadatha kuchitapo china chake kuonetsa kuti wakhumudwa kuti inuyo ndi amene mwamupatsira kachilomboko. Pali malamulo mdziko muno, oti wina akapatsira mnzake kachilombo ka HIV mwadala, ameneyo ali ndi mlandu. Ndithu, pitani nayoni nkhaniyi kwa odziwa malamulo kuti akuthandizeni. +Adona Hilida afika pa Wenela Adafika pa Wenela tsikulo Abiti Patuma akuimba nyimbo yatsopano ya Lucius Banda. Inde ija waimba ndi Thocco Katimba: Mwandikumbuka. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Yahwe, wandimasula Wandimasula Yahwe wandimasula Wandipepesa Yahwe wandipepesa Nditi zikomo Yahwe wandimasula Ndinu patali. +Koma isanathe nyimboyo, wapamalo aja timakonda pa Wenela, Gervazzio, mnyamata wa ku Nkhotakota, adaika nyimbo ina ya mkulu wa kwa Sosola uja. +Kudali kuthyola dansi mkati mwa usiku. Musandifunse kuti nthawi idali bwanji chifukwa sindikuuzani. Ndipo mukadziwa mukufuna mutani? Idali nthawi yotaika basi. +Dansi ili mkati, mdima utafika pena, tidangoona kunja kukuwala ngati msana! Aliyense adanthunthumira. +Kutuluka panja, tidaona mzimayi ali palichero. Mzimayiyo adaponya nsalu imene idali paphewa pake pansi. Idali kufuka moto lawilawi ngati dziko la Malawi, dziko lamoto. +Tonse tidanthunthumira. +Posakhalitsa, ndegeyo idatera. Mayiyo adatsika. +Osandiopa, ndine wanuwanu Dona Hilida. Mumati sindigabwere kuno kumudzi? Ndabwera kudzaona mbale wanga Pitapo. Mudziwa adandigawirapo mawiribala 50 mmbuyomu, adayamba nkhani. +Mitima idakhalako pansi. Koma nanga munthu akafike pa Wenela pandege yausiku? Kodi kuchoka ku Zambia kufika pa Wenela kulibe basi? Izo zili apo, kudzera ku Zambia kuchokera ku Jubeki si kudzitalikitsa? Ayi ndithu, abale anzanga, tizionera limodzi. +Tsono bwanji mukubwera usiku chonchi? Nanganso bwanji mukubwera pamene mwana wanu Pitapo akufuna kuweruzidwa? adafunsa Abiti Patuma. +Mukumuzunziranji Pitapo? Simukuona akuzunzika? adafunsa Adona Hilida. +Taonani momwe abambo ovala nkhwaira, amene amayi awo adamwalira kaamba kosowa mankhwala akuzunzikira pomunyamula pamachira aja adanyamulira Listonia Susi ndi Chuma kalelo, adatero Abiti Patuma. +Koma, abale, inetu palibe chimene ndimatolapo pankhani zawozo. Kodi nanga ndidapondapo ku Nyumba ya Malamulo? Inetu Nyumba ya Chimfiti ku Zomba sindiyidziwa. Za Chingwes Hole, Emperors View ngakhalenso Mulunguzi Dam, inde koona nsomba za trout komanso mpandankhuku, ndimangomva mwa anthu. +Koma mayi, simungachititse msonkhano masana pa Nyambadwe pompa? Kuchoka pano pa Wenela simungathe mphindi 10, ndidatero. +Ndidaonjeza: Mukadzangoti mwafika pa Chimsewu, ndidzakuimbirani nyimbo ija ya Adona Hilida! Wa-wa-wa-wa. Komanso: Tulutsani wanuyo, timuone, ngati si dona, ife wathu ndi dona! Ngakhale ndikudziwa Moya Pete zikumulaka, nthawi yanga sinakwane. Mundiona ndibwera. Kugona kozizira ndakana. Inetu sangandipatse belo muja adachitira Kakali wathawa uja! adayankha Adona Hilida. +Koma, abale, kunjaku kuli zigawenga. Zoona kuthawa belo! Koma Kakali! Ndikumvatu kuti mnyamata ameneyu si pano. Sachita nawo za mowa, koma amagulira ena mkati mwa usiku. Mwina timaona afika pa Wenela ngati sanalowere ku Zobue kukaletsa nkhondo ya Renamo. +K5 biliyoni yothana ndi matenda a mkungudza Bungwe la Queen Elizabeth Diamond Jubilee Trust (QEDJT) lapereka ndalama zokwana K5 biliyoni kuboma la Malawi zogwirira ntchito yothetsa matenda a khungu otchedwa mkungudza (trachoma) mdziko muno. +Potsimikiza nkhaniyi, mneneri wa unduna wa zaumoyo, Adrian Chikumbe, wati boma ligwira ntchitoyi ndi mabungwe angapo, kuphatikizapo lodziwika bwino mdziko muno la Sightsavers, lomwe lidalandira ndalamazi. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Ntchitoyi, yomwe adaikhazikitsa kale mdziko muno mu October chaka chathachi mboma la Karonga, akuti idya ndalama zokwana K5.110 biliyoni mzaka zinayi zomwe akhale akuigwira. +Koma Chikumbe adauza Tamvani kuti ngakhale kuti dziko lonse la pansi laika 2019 ngati chaka chothetsera matendawa, boma la Malawi ligwira nchitoyi mwachangu komanso molimbika kuti pofika 2018 matendawa adzakhale atatheratu mdziko muno. +Nthawi yoti matendawa adzakhale atatheratu padziko lonse la pansi ndi chaka cha 2019, koma kuno ku Malawi taganiza kuti tichite chamuna pothana nawo chisanafike chaka chimenecho, adatero Chikumbe. +Mkuluyu adatinso pakalipano matendawa avuta kwambiri mmaboma okwana 15. Pachifukwachi, bungwe la Sightsavers akuti layamba kale kugwira ntchitoyi, maka mmaboma omwe akhudzidwawo. +Iye adati ntchito yogawa mankhwala kwa odwala nthendayi ifalikira madera onse a dziko lino posachedewapa ndi cholinga chothana ndi matendawa msanga. +Panopa, maboma omwe akhudzidwa kwambiri ndi nthendayi ndi a Kasungu, Nkhotakota, Salima, Karonga, Mchinji, Lilongwe, Zomba, Machinga, Mangochi, Ntcheu, Nsanje, Neno, Mwanza, Dowa ndi Ntchisi, adatero Chikumbe. +Nalo bungwe la Sightsavers, lomwe ndi akadaulo odziwa bwino za ntchitoyi, lati dziko la Malawi lili mgulu la maiko oyambirira okwana 14 padziko lapansi omwe akuvutika kwambiri ndi matenda a mkungudzawa. +Pafupifupi anthu okwana 230 miliyoni omwe akudwala matendawa padziko lapansi, 9.5 million ali ku Malawi, latero bungwe la Sightsavers. +Malinga ndi a Sightsavers, ntchitoyi akuti ikayambika agawa mankhwala kwa anthu oposa 8 miliyoni mdziko muno. +Mchikalata chake, bungweli lati matenda a mkungudza ngakhale kuti ndi ochizika, ndi osautsa kwambiri kotero kuti ngati munthu achedwa kulandira chithandizo msanga akhoza kupunduka ndi kukhala wakhungu. +Bungweli lati zina mwa zizindikiro za nthendayi ndi zakuti zikope nthawi zambiri zimagwera mkati mwa diso, kenaka nsidze zimayamba kukanda galasi la disolo mpaka kuchita zilonda. Ndipo zinthu zikafika pamenepo munthuyo sangathenso kuona. +Bungweli lati nthendayi, yomwe ndi yopatsirana, imafala mofulumira ngati anthu ambirimbiri akhala malo othinana, komanso opanda ukhondo wokwanira. +Malinga ndi a Sightsavers, bungwe la zaumoyo padziko lonse la pansi la World Health Organisation ndi lomwe lidavomereza kuti ntchito yotereyi ichitike ndipo maiko ena omwe ntchito yamtunduwu ichitikenso ndi Kenya, Uganda, Nigeria ndi Mozambique. +Osataya za makolo Kulosera nyengo nkotheka Pamene zikuoneka kuti ngozi zina zadzidzidzi zimene zakhala zikuchitika kaamba kolephera kulosera kubwera kwa ngozi zotere, boma lapempha Amalawi kuti alimbikire kugwiritsa ntchito njira za makolo polosera momwe mvula ingagwere. Pamene nkhani yolosera mvula ili mkamwamkamwa, boma lati lili pakalikiliki kuti madzi osefukira amene amasautsa mmadera ena chaka chino lisakhale vuto la mnanu. +Chisale watuluka nkumangidwanso Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Mumzinda wa Blantyre mudaoneka nkhokwe iyi Ambiri mwa anthu omwe amakhudzidwa ndi omwe amakhala mmphepete mwa madzi makamaka mmaboma a kuchigwa cha Shire: Chikwawa ndi Nsanje. Chaka chatha kusefukira kwa madzi kudankitsa ndipo kudakhudza maboma 18 mdziko muno, mpaka mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adati dziko lino ndi la ngozi, zimene zidachititsa kuti mabungwe ndi maiko athandizepo. +Malinga ndi mkulu wa nthambi yoona ngozi za dzidzidzi Bernard Sande, chomvetsa chisoni nchakuti ngozi zotere zikachitika boma limaononga ndalama za nkhaninkhani kusamala anthu okhudzidwawo ndi kubwezeretsa zinthu zoonongeka. +Chaka chino chokha Koma bomalo lati sikuti likutaya njira za sayansi zolosera zanyengo. +Mlembi wa mkulu wa thambi yoona za ngozizi Bernard Sande adati ngozi zina monga kukokoloka ndi madzi osefukira zingapewedwe potsatira zizindikiro zachilengedwe. Iye adati kalekale makolo amalosera zobwera mtsogolo pogwiritsa zizindikiro zachilengedwe ndipo zimawayendera. +Pali zizindikiro zina monga kalilidwe kambalame, mmene mitengo yayangira masamba ake, kaombedwe kamphepo ndi mmene kwatenthera kapena kwazizirira chaka chimenecho zomwe makolo amaloserera mmene mvula igwere, adatero Sande. +Iye adatinso utawaleza ukaoneka kumwamba utazungulira mwezi kapena dzuwa zomwe ena amati nkhokwe, makolo amakhulupirira kuti chaka chimenecho kugwa mvula yambiri ndiye amakonzekera mokwanira. +Lamulungu lapitali [pamwambo wokumbukira za ngozi zodza mwadzidzidzi] imodzi mwa nkhani zomwe zidakula ndi ya nkhokwe yomwe anthu ambiri omwe adalankhulapo adati ndi chizindikiro chakuti kubwera mvula yambiri, adatero Sande. +Polankhula ndi Tamvani Lachitatu, T/A Maseya wa mboma la Chikwawa adati nkhani yazizindikiro za kubwera kwa mvula yambiri ndi yoona ndipo zizindikirozi zimagwirabe ntchito mpaka pano. +Iye adati chaka chatha anthu ena kuchigwa cha Shire adadziwiratu kuti kubwera mvula yochuluka chifukwa kuoneka chiganganthila (chinyama chooneka ngati ngona koma cha mlomo wautali). +Maseya adati chinyamachi chioneka ndi chizindikiro chakuti chaka chimenecho kugwa mvula yoopsa ndipo anthu amachitengera kwa amfumu omwe amadziwa kupha kwake. +Zizindikiro zina ndi kutentha; kukatentha moonjeza timadziwa kuti kuvuta, adatero Maseya. +Mfumuyo idavomereza kuti nkhokwe nayo ndi chizindikiro chakuti chaka chimenecho mvula igwa yamphamvu komanso zokolola zikhala zambiri. +Paramount Kyungu wa ku Karonga adati nthawi yodalira zizindikiro za makolo polosera kabweredwe ka mvula idapita ndipo masiku ano ndiwofunika kutsatira zomwe akatswiri a zanyengo anena. +Kyungu adati kalelo kudali anthu ake omwe amadalirika pankhani zoloserazo omwe adamwalira kalekale choncho nkunamizana kunena kunena kuti anthu angadziwe zobwera pogwiritsa ntchito zizindikiro zachilengedwe. +Katswiri wa za sayansi ya za nyengo kusukulu yaukachenjede ya Chancellor College Cosmo Ngongondo adati zizindikiro monga nkhokwe zimachitika kaamba ka zochitika mlengalenga. +Iye adati sikuti zoterezi zikaoneka ndiye kuti ayembekezere mvula yambiri koma kuti mwamwayi zimangochitika kuti mvulayo yagwadi yambiri malingana ndi mmene mlengalenga mulili. +Nkhokwe imaoneka kukakhala mitambo yomwe pa sayansi imatchedwa cirrus ndipo mitambo imeneyi siyibweretsa mvula koma chomwe chimachitika nchakuti mitamboyi imatsogozana ndi mtundu wa mphepo yomwe imabweretsa mvula. +Pachifukwa ichi kumapezeka kuti mitambo ya Cirrus ija ikakhalako, mwayi wakuti mphepo yogwetsa mvula ikhalako umakula ndiye zikatero anthu amangoona ngati nkhokweyo ndiyo imabweretsa mvula yambiri, adatero Ngongondo. +Iye adati nkhokwe imachitika pomwe kuwala kwa dzuwa kapena mwezi kwanjanja mmadzi ouma omwe amapezeka mmitambo ya cirrus ndipo kuwala konjanjako kumabalalika mmitundu yosiyanasiyana yomwe imakhala mmbalimmbali mwa dzuwa kapena mwezi. +Mwangonde: Khansala wachinyamata Akamati achinyamata ndi atsogoleri a mawa, ambiri amaganiza kuti izi ndi nkhambakamwa chabe. Koma achinyamata ena, monga Lusubilo Mwangonde, akukwaniritsa akupherezetsa mawuwa osati pongolota kuti adzakhala, koma kutsogolera kumene chifukwa nthawi yawo yakwana. DAILES BANDA adacheza ndi Mwangonde, khansala wachinyama, yemwe akuimira Jumbo Ward mumzinda wa Mzuzu, motere: Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ali ndi masomphenya: Mwangonde Tikudziweni Ndine Lusubilo Mwangonde, ndili ndi zaka 27 zakubadwa. Ndinabadwa mbanja la ana asanu ndipo ndine wachinayi kubadwa. Ndimachokera mmudzi mwa Mwamalopa, kwa Paramount Chief Kyungu mboma la Karonga. Sindili pabanja pakadalipano. +Mbiri ya maphunziro anu ndi yotani? Maphunziro anga a pulaimale ndidachitira kusukula yapulaiveti ya Viphya mumzinda wa Mzuzu ndipo asekondale ndidachitira pa Phwezi Boys mboma la Rumphi. Ndili ndi diploma ya Accounting ndipo pakadalipano ndikupanga digiri komanso Chartered Accounting kusukulu ya Malawi College of Accountancy (MCA). +Mudayamba bwanji zandale? Kuyambira ndili wachichepere, zaka 12, ndakhala ndikukhala mumaudindo a utgogoleri. Ichi ndi china mwa zinthu zomwe zidandilimbikitsa kuti ndikhoza kudzapambana pazisankho. Koma chachikulu chomwe chidandichititsa kuti ndilowe ukhansala chidali chifukwa chakuti ndinkafuna kupereka mpata kwa anthu kuti azitha kuyankhula zakukhosi kwawo polimbikitsa demokalase ndi chitukuko. +Ntchito mukugwira ndi zomwe munkayembekezera? Eya, ndiponso ndinkayembekezera zambiri. +Masomphenya anu ndi otani pandale? Ine ndine munthu wokhulupirira Mulungu ndipo ndili ndi chikhulupiriro choti Iye ndi amene adzandionetsere zomwe ndikuyera kuchita ndi tsogolo langa. +Zinthu zina zomwe mumachita ndi chiyani pambali pa ukhansala? Ndikakhala sindikugwira ntchito yaukhansala ndimakhala ndikuchita bizinesi, nthawi zina ndimakhala ndili kusukulu komwe ndikuchita maphuro anga a digiri. Kuonjezera pamenepo ndili ndi bungwe lomwe ndidayambitsa ndi anzanga ena la Centre for Participatory Democracy lomwe limalimbikitsa demokalase. +Zomwe mwakwanitsa ndi zotani? Ndathandiza kuti ntchito yopala misewu ya kudera la Moyale itheke. Misewuyi yakhala nthawi yaitali osapalidwa. Ndidathandiziranso kuti ochita malonda ayambe kumanga mashopu anjerwa ndi kusiya kumangira matabwa kapena zigwagwa. Ndidakwanitsanso kukaimirira khonsolo ya Mzuzu ku Nyumba ya Malamulo. Ndaonanso kuti ntchitoyi yandithandiza kusintha momwe ndimaonera zinthu komanso ndimakumana ndi anthu osiyanasiyana omwe amandiphunzitsa zinthu zambiri. +Kudali Ku Karonga Pamene ena amati chikondi sichiona chikhalidwe kapena mtundu wa khungu la munthu, banja la Manaseh Chisiza, mkulu wa bungwe la azisudzo ndi mkazi wake Andrea Beyerlein likuchitira umboni mawuwa. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Manaseh, mkulu wa National Theatre Association of Malawi, adakumana ndi njole yake ku Karonga komwe Andrea adabwera ndi makolo ake kuyendera ntchito zachifundo zomwe iwo adali kugwira mogwirizana ndi bungwe lina la ku Mzuzu. +Manaseh ndi Andrea tsiku la ukwati wawo Atabwera nthawiyo adapezeka kuti adafikanso ku Lusubilo Orphan Care Project komwe ndidamuona koyamba, adatero Manaseh, yemwenso ndi mkulu wa gulu la zoimb la Lusubilo Band. +Awiriwa adapatsana nambala za telefoni ndipo ankachezerana kufikira pomwe adakumananso ku Germany chaka chathachi. +Kukumana kwawo ali ku Germany kudali chiyambi cha chikondi chomwe chidakula ndipo chikukulirakulirabe mpaka adamanga woyera mwezi watha ku Germany komweko. +Manaseh adati Andrea yemwe ndi woimba komanso wochita mafilimu amalemekeza chikhalidwe chake Chimalawi ndipo banja lawo limaganizira zikhalidwe zonse za Chizungu komanso chikhalidwe cha Chimalawi. +Andrea amakonda kukonza mnyumba pomwe ine ndimakonda kuphika osati chifukwa cha chikhalidwe cha kwawo koma chifukwa ndimakonda kuphika basi kuyambira kalekale ndipo ndimaphika bwino kwambiri, adatero Manaseh. +Manaseh ndi wochokera mmudzi mwa Khwawa T/A Mwasambo mboma la Karonga ndipo adabadwa mbanja la ana 8 momwe ndi wachisanu ndi chimodzi kubadwa. Andrea adabadwa yekha mbanja la kwawo. +Ntchito yasowa, wayamba ulimi wa kabichi Adabwera mtauni ya Blantyre kudzasaka ntchito atamaliza Fomu 4. Adaponda paliponse kukasaka ntchito, makalata chilembelenicho ndi satifiketi yake ya Malawi School Certificate of Education (MSCE) koma palibe amene adamutenga. Yankho lidali lobwerera kumudzi kuti akangoyamba ulimi. Lero ulimi wa kabichi wayamba kumupatsa ndalama, wagula ngombe ziwiri, njinga, nkhuku komanso wamangitsa nyumba. Iyi ndiyo nkhani ya Patrick Khuliwa, yemwe akucheza ndi BOBBY KABANGO. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Kodi tingachezeko, wawa? Kwambiri, palibe choletsa. Kaya mufuna ticheze nkhani zanji potitu tangokumana kumunda kuno. +Mbiri yanu komanso ulimi wa kabichi Vuto palibe, uwu ndi munda wanga, ndalima ndekha ndiye palibe pamene pangandivute kufotokoza. +Khuliwa akuti watola chikwama muulimi wa kabichi Koma mbiri yanu ndi yotani? Ndimachokera mmudzi mwa Mulunguzi kwa T/A Juma mboma la Mulanje. Ndili ndi satifiketi ya Fomu 4 yomwe ndidapeza mu 2007. Nditakhoza, ndidapita ku Blantyre monga ambiri amachitira komwe ndimakasaka maganyu. Achimwene, ndidavutika osati masewera, ntchito zikusowa. Zoti ndakhoza mayeso a Fomu 4 ngati bodza, ena ake amati mwina ndiyese ntchito za mnyumba koma malipiro ake adali ochepa. Mapeto ake ndidabwerera nkudzayamba ulimi wa kabichi. +Ulimiwu mudayamba liti? Mu 2007 momwemo nditabwerako kutauni. +Chaka chino mwalima munda wokula bwanji? Nanga mukupeza zotani? Ndalima theka la ekala. Munda umenewu chaka chino ndakolola matumba 20 a kabichi olemera makilogalamu 100 lililonse. +Mwapha ndalama zingati? Thumba limodzi ndimagulitsa K9 000, pamatumba 20 ndidapeza K180 000 koma kabichi wina ndimagulitsira kumunda konkuno. +Msika mumaupeza bwanji? Panopa palibenso nthawi yokayangana msika chifukwa mavenda akumadzagula kumunda konkuno koma chomwe tikuonetsetsa nchakuti mtengo uzikhala wabwino. Monga poyamba timagulitsa K7 000 pa thumba limodzi koma pano lachita kukwera. +Pa chaka mukumalima kangati? Nthawi ya mvula ndimalima kamodzi, koma mvula ikangotha ndimalima kabichi wamthirira yemwe ndikumalima kawiri, kusonyeza kuti ndikumalima katatu. +Uyu ali mmundayu ndi wachingati? Wachiwiri. Ndayambanso kukolola moti sabata ino ndikumaliza kukolola ndipo ndayamba kale kulima wina. Kutereku mbali inayo ndabzala kale. Pofika December ndikhala ndikukolola kusonyeza kuti ndidzakhala ndikukonzekera ulimi wa mvula. +Ulimi woyamba ndi wachiwiriwu mwapeza ndalama zingati? Kupatula zochotsachotsa, ndalama yogwirika yomwe ndidaisunga idalipo K250 000. Ndalama zinazo ndimagwiritsira ntchito pakhomo. +Chiyambireni ulimiwu mwapangapo chiyani? Ndamangitsa nyumba ya njerwa zootcha yomwenso ndi yamalata; ndagula ngombe ziwiri ndipo ndikulankhula pano zili mkhola mwake; komanso ndili ndi nkhuku ndi njinga. Ntchito zapakhomo zikuyenda kuchokera mkabichi yemweyu. +Bullets iphana ndi Wanderers lero Ambiri adakamba kuti mwina masewero a lero pakati pa Bullets ndi Wanderers mu TNM Super League alephereka ponena kuti osewera akukatumikira Flames, koma izo ndi nkhani yakale chifukwa lero ntchito ilipo pa Kamuzu Stadium. +Kochi wa Flames Ernest Mtawali Lachinayi adawalola osewera kuti akatumikire matimu awo. Osewerawo adangololedwa kuti asewere masewero alero ndipo abwerere ku Flames madzulo alero. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Bullets idachinya Wanderers mndime yoyamba 2-1 ndipo Wanderers idabweza chipongwe mu Carlsberg Cup pamene idapambana 2-1. +Lero kamuna ndani? Mphunzitsi wa Wanderers Elijah Kananji akuti timu yake yakonzeka ngakhale palibe osewera monga Jabulani Linje ndi Rafiq Mussa chifukwa chovulala. +Pamene Mabvuto Lungu wa Bullets akuti nawonso akonzeka komabe timu yawo isowa ntchito za Chiukepo Msowoya, Owen Chaima ndi Vincent Gona chifukwa chovulala pamene Sankhani Mkandawire wabwerera. +Namrukhunua: Nyumba ya chilhomwe Kalelo makolo adali ndi njira zawo zochitira zinthu kuti azisangalala ndi kukhala wotetezedwa. Alhomwe nawo ali ndi zimene makolo awo adayambitsa ndipo zina zimapitirirabe mpaka pano. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi wotsata chikhalidwe cha Alhomwe mumzinda wa Lilongwe, Fustafu Mbewe. Adacheza motere: Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Pa mtundu wa Alhomwe pali mawu akuti Namurukhunua, kodi tanthauzo lake nchiyani? Imeneyi ndi nyumba yozungulira yomwe makolo pa mtundu wa Chilhomwe adayambirira kumanga kalelo nkumakhalamo. Kanyumba kameneka kamakhala kakangono ndipo kamakhala kopanda chipinda. +Pomanga amagwiritsa ntchito zipangizo zanji? Timagwiritsa ntchito mitengo, tsekera, khonje, zilambe, matope ndi namgoneka (zokhala ngati zilambe ndipo ena amalukira mipando). Masiku ano enanso amagwiritsa ntchito misomali. Chitseko chimakhala cha kaphe, kabala wake mtengo omwe umapingasa pachitseko. +Ndiye mwati imakhala nyumba yaingono, mumakhala anthu angati mmenemo? Namrukhunua mumakhala anthu awiri (banja) ndipo ngati pali wachitatu ndiye kuti ndi mwana wa mnyumbamo. Ngati pali anthu ambiri, amamanganso tinyumba tambiri pamodzimodzi ngati banja limodzi koma katundu yense wakukhitchini, ziwiya za madzi ndi madengu a ufa amakhala mnyumba momwemo. +Pomanga zimakhala bwanji? Pamalo akasosapo bwinobwino amatenga chingwe ndi mitengo nkuyamba kuyeza muja amachitira akafuna kumanga nkhokwe. Akakwanitsa kupimako, amazika mitengo mmphepetemo ndikuyamba kuphoma ndi matope ndipo akamaliza amafolera ndi tsekera nkukonza chitseko. +Pachibale pawo akalakwirana nkhani zake zimayenda bwanji? Monga ndanena kale, pachibale amamanga nyumba zawo pamodzimodzi kupatula makolo, omwe amamanga patali pangono koma poonekera ndiposavuta kufikapo. Pakachitika mapokoso, amakauza makolo olo ngati zili za mbanja, amauza ankhoswe ndikukamba koma zikalephera ndiye zimakafika kwa amfumu kuti athandizepo. +Nanga amuna a Chilhomwe zida zawo ndi chiyani? Alhomwe zida zawo ndi chikwanje (koma chimakhala ndi ngowe), nsompho (nkhwangwa) ndi mpeni omwe amautchinjiriza ndi kachikwama kopangidwa ndi chikopa cha nyama. Mpeni wa Mlhomwe suonekera chisawawa amaubisa ndipo umatuluka pokhapokha ngati ukufunika kuti ugwire ntchito. +Alhomwe ntchito yawo yaikulu ndi chiyani? Alhomwe amakonda kulima. Mbewu zomwe amakonda kulima kwambiri ndi kalongonda, chinangwa, nandolo, mbatata, nzimbe, chimanga, mapira ndi tchana. Chakudya chawo chodalilika ndi nsima ndi zipatso; amakondanso nandolo osakaniza ndi makaka. +Nanga mavalidwe awo? Amayi a Chilhomwe amakonda kuvala nsalu, andiloko (iyi ndi siketi yaitali yomwe ena amati makisi), bulauzi ndi mpango ndipo amakonda kusokera nsalu ya biliwita (yakuda). Abambo amakonda kabudula ndi malaya osokedwa ndi nsalu ya khaki. +Tangomalizani ndi ena mwa magule otchuka pa chilhomwe. +Pali magule monga tchopa, sekhere ndi jiri. Povina Tchopa amavala zikopa za nyama komanso amaberekera tinthu tokhala ngati nyama kumsanaku mmiyendo muli mawerewesa oti azipanga kaphokoso povina. Povina sekere amavala mikanda paliponse ndi mkhosi momwe komanso amadzikongoletsa nkhope yonseyi. Jiri ndi gule yemwe amavinidwa usiku kuli mwezi ndipo amavina ndi amuna ndi akazi. Mwachidule magule ndiye alipo ambiri osangalatsa pa mtundu wa Alhomwe. +Muva: Kutsitsimutsa anthu mukuimba Lero Lamulungu akuyembekezeka kukakhazikitsa chimbale chake cha Messiah 1 ku Mzuzu pa Boma Park. Kumeneko kukakhala oimba osiyanasiyana odziwika mMalawi muno. DAILES BANDA adacheza ndi Donnex Muva kuti amudziwitsitse mkuluyu, yemwe akuti cholinga chake nkutsitsimutsa anthu kudzera mu nyimbo. Adacheza naye motere: Akhazikitsa chimbale chake lero: Muva Tikudziweni achimwene. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ndine Donnex Muva ndipo ndimachokera mmudzi mwa Kajani kwa Inkosi Kampingo Sibande mboma la Mzimba. Ndili ndi zaka 32 zakubadwa, ndili pabanja ndipo ndili ndi ana atatu. +Mbiri ya maphunziro anu njotani? Ndayenda sukulu zambiri kaamba ka bambo anga omwe ndi abusa, koma mayeso anga a Sitandade 8 ndidalembera ku Chihami mboma la Nkhata Bay ndipo sekondale ndidaphunzira ku Chintheche mboma lomwelo. +Nditamaliza sekondale ndidachita mwayi woyamba ntchito ku Chipiku koma pakadalipano ndikugwira ntchito kubungwe la Solar Aid Malawi. +Mudayamba bwanji kuimba? Kuimba ndidayamba ndili wachichepere kwambiri, makamaka kaamba ka ubusa wa bambo anga. Panthawiyo ndinkaimba mukwaya ya kumpingo kwathu. Kuimba kwenikweni ndidayamba mchaka cha 2009 pomwe ndidatulutsa chimbale choti Nthawi ya Manna Inatha. +Chaka chino ndikuyembekezeka kukakhazikitsa chimbale changa cha Messiah 1 ku Mzuzu ku Boma park pa 30 August. Kumeneko kukhalanso oimba osiyanasiyana odziwika mMalawi muno. +Zomwe mwakwaniritsa pamoyo wanu ndi ziti? Chachikulu chomwe ndakwaniritsa ndi kubweretsa anthu kwa Mulungu kudzera mu nyimbo komanso kukhala ndi zimbale ziwiri si chinthu chapafupi chifukwa kupanga chimbale pamalowa ndalama zambiri. +Pali zopinga zotani zomwe mwakumanapo nazo? Zopinga ndiye zilipo, choyamba ndi mchitidwe woba nyimbo moti ndikunena pano anthu ayamba kale kubena nyimbo zanga. Mchitidwewu umabwezeretsa kwambiri mmbuyo anthu oimbafe. Chachiwiri ndi kusowa kwa chithandizo popanga chimbale. Monga ndanena kale, ndalama zimalowa zambiri pantchito yapanga chimbale, zomwe oimba ambiri sitingakwanitse patokha ndipo timafuna chithandizo kuchokera kwa makampani akuluakulu monga zimakhalira kumaiko ena. +Oimba anzanu muwauza zotani? Pakhale chikondi pakati pathu osati kuponderezana. Ndi mtima wofuna kukhala pamwamba nthawi zonse womwe ukuononga oimba ambiri mdziko muno. +Wopezeka ndi yunifomu ya polisi anjatidwa Apolisi ku Zomba akusunga mchitolokosi bambo wa zaka 25 pomuganizira mlandu wopezeka ndi yunifomu ya polisi komanso mfuti popanda chilolezo. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Nyaude: Tidadabwa ndi zochitika zake Mneneri wa polisi kuchigawo chakummawa, Thomeck Nyaude, watsimikizira za nkhaniyi ponena kuti adanjata Clement Mawerenga wa mmudzi mwa Katete, T/A Malemia pamsika wa Songani. +Tidadabwa ndi zochitika za mkuluyu ndipo titamuyandikira tidaona kuti sadali wapolisi ngakhale adapezeka ndi katunduyo. Adali ndi malaya komanso mabuluku a polisi 12 kuphatikizapo mfuti, adatero Nyaude. +Kuchigawo chakummawa komweko, apolisi mboma la Machinga atsekera amuna anayi powaganizira mlandu woba katundu wa K3.7 miliyoni. +Nyaude adati anthuwa akuwaganizira kuti adaba mapaipi 244 a madzi ndi zipangizo zina kwa White Mbalame, wa mmudzi mwa Kawinga, kwa T/A Kawinga mbomalo. +Nyaude adati amene akuwaganizira za mlanduwu ndi Madalitso Wasi, Andrew Amin, White Samson ndi Christopher Chapita. +Tikuwaganizira kuti adapalamula mlanduwu mu November 2013. Titangowamanga, tapeza mapaipi 160, adatero mneneriyu. +Chikondi cha nkhwangwa DPP, UDF akumana pachisankho chachibwereza Ubale wa pakati pa chipani cholamula cha DPP ndi chotsutsa cha UDF mNyumba ya Malamulo, womwe umaoneka ngati ukhala wa mpakana imfa kuwalekanitsa, wayamba kuwonekera mawanga ake. Zipanizi zanenetsa kuti aliyense aima payekha mchisankho cha makhansala chachibwereza chikubwera mwezi wamawawu. +Kasaila: Aliyense aona za mchipani chake Mneneri wa chipani cha DPP, Francis Kasaila, wauza Tamvani kuti palibe mgwirizano uliwonse pakati pa zipani ziwirizi kunja kwa Nyumba ya Malamulo monga momwe anthu ambiri amaganizira. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Polankhua Lachitatu lapitali, Kasaila adati pachisankho chomwe chichitike pa 25 August, chipani chilichonse chili pachokha ndipo aimiriri awo adzakumana maso ndi maso. +Aliyense aona za mchipani chake chifukwa mgwirizano womwe ulipo ndi wothandizana mNyumba ya Malamulo basi, osati kunja. Chipani chilichonse chipanga ganizo pachokha kuimitsa munthu kapena ayi, koma palibe zoimitsa munthu mmodzi [kuimira zipani ziwirizi], adatero Kasaila. +Naye mneneri wa chipani cha UDF, Ken Ndanga, adati chipani chawo chikupanga zake pankhani yokhudza chisankho chachibwerezachi. +Ndanga adati pakalipano atsogoleri a chipani cha UDF mmaboma akuyendetsa zonse zokhudza kukonzekera chisankhochi ndipo a kulikulu adzalandira maina a omwe adzaimire chipanichi posachedwapa. +Palibe mgwirizano uliwonse wokhudza za chisankho. Ubale nku Nyumba ya Malamulo basi, kunja kuno aliyense ali ndi zake moti kukutsimikizirani pachisankhochi tidzaimitsa makandideti athu, adatero Ndanga. +Katswiri wa za malamulo Edge Kanyongolo adati mgwirizano wa zipanizi sukuwamanga chifukwa sadasayinirane paliponse koma adangokambirana basi. +Iye adati zipanizi zili ndi ufulu wosankha odzaziyimirira mmodzi kapena aliyense kukhala ndi odzaimirira wawo popanda chiletso chilichonse. +Palibe chowamanga chifukwa mgwirizano wake sudalembetsedwe. Zili ndi eni ake kukambirana ndi kumvana chimodzi, adatero Kanyongolo. +Mneneri wa bungwe loyendetsa zisankho mdziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC), Sangwani Mwafulirwa, adati bungweli silikhudzidwa ndi kasankhidwe ka opikisana nawo pachisankho. +Ife sitilowerera nawo pankhani imeneyo. Chomwe ife timayangana nchakuti opikisana nawo ankhale ndi chizindikiro, basi, kaya akuima payekha kaya akuyimira chipani kapena mgwirizano, akuyenera kukhala ndi chizindikiro, adatero Mwafulirwa. +Chipani cha UDF chidasankha kugwira ntchito ndi chipani cha DPP mNyumba ya Malamulo ndipo nkhaniyi idachititsa kuti mabungwe komanso zipani zina zipemphe sipikala wa nyumbayi kuti achotse aphungu 11 a UDF potsatira gawo 65 la malamulo a dziko lino, koma mpakana pano sipikalayu sadagamule chilichonse pankhaniyi. +Gawoli limati phungu yemwe adali mchipani china panthawi yakusankhidwa kwake adzasiya udindowu ngati walowa chipani china chomwe chilinso mNyumba yomweyi. +Mmodzi mwa akuluakulu a mabungwe omenyerera ufulu wa anthu, Billy Mayaya, adalembera kalata sipikala wa Nyumba ya Malamulo, Richard Msowoya, kuti aphunguwo adaphwanya gawo 65 ndiye achoke mNyumbayi. +Mneneri wa chipani cha MCP, Jessie Kabwila, naye adati mpovuta kuti aphunguwo akhalebe mNyumbayi chifukwa mbali yawo yeniyeni sikudziwika. +Chipani cha UDF chidakana kuti aphungu ake asintha chipani koma adangoganiza zogwira ntchito ndi chipani cholamula cha DPP, basi. +Chilengezereni nkhaniyi, chipani cha UDF chidalandidwa ufulu woyankhapo pankhani za boma ngati chipani chotsutsa boma mNyumba ya Malamulo. +MEC idatulutsa ndondomeko ya momwe chisankho cha chibwereza cha mmadera 5 chidzayendere ndipo ikuyenera kumaliza kulandira zikalata za odzapikisana nawo pa 28 July uno. +Mwafulirwa adati zokonzekera zonse zikuyenda bwino ndipo anthu ayembekezere chisankho chapamwamba ngakhale kuti bungweli lili ndi ndalama zochepa zoyendetsera chisankhochi. +Chisankho chonse chimafunika K400 miliyoni ndipo ife tili ndi K141 miliyoni koma palibe chogwedeza chilichonse. Zonse zidzayenda bwinobwino, adatero Mwafulirwa. +Mmadera momwe muchitike chisankhochi ndi Luchenza, dera la pakati ku Zomba, Msikiti ku Mangochi, Chibanja ku Mzuzu ndi Khwawa mboma la Karonga. +Mtima pansi, mayeso A jce alipo chaka chino Ngati panali kupeneka kulikonse kuti chaka cha 2015/16 kukhala kapena sikukhala mayeso a Junior Certificate of Education (JCE) kutsatira zomwe boma lidalengeza posachepadwa kuti lathetsa mayesowo msukulu za sekondale, kukaikako kutheretu chifukwa boma latsimikiza kuti mayesowo alembedwa. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Escom in free-for-all fuel scam Eni sukulu zomwe si zaboma akhala akudandaula kuti boma lawaika pachingwe cha kangaude polephera kubwera poyera ndi kufotokoza ngati mayesowo aliko kapena ayi zitangomveka kuti boma lathetsa satifiketi ya JCE, koma osamasula kuti zimenezi ziyamba liti. +Ophunzira kulemba mayeso a JCE mmbuyomu Mneneri wa unduna wa zamaphunziro, Manfred Ndovi, wati pasakhale mpungwepungwe uliwonse pankhaniyi poti mayesowa aliko koma kuyambira chaka cha mawa cha 2017 mayesowa sadzalembedwanso. +Mayeso aliko! Chaka chino chikhala chomaliza kulembetsa mayeso a JCE koma kuyambira chaka cha 2017 sikudzakhalanso mayeso oterewa, adatero Ndovi pouza Tamvani palamya. +Iye adati sukulu ndi ana onse omwe ali Fomu 2 ndipo akuyembekezera kulemba mayeso a JCE, atsatire ndondomeko zonse zoyenerera pokonzekera mayesowa, osati kutekeseka. +Mkulu wa bungwe la eni sukulu zomwe si zaboma, Joseph Patel, adauza Tamvani kumayambiriro a sabatayi kuti eni sukuluzi akusowa kolowera pankhaniyi kaamba kakuti sakudziwa ngati mayesowa alembedwe chaka chino kapena ayi. +Boma lidaganiza zoyambitsa njira yosefera ophunzira potengera momwe akuchitira mkalasi komanso pamayeso a teremu iliyonse mmakalasi onse kulekeza Fomu 3 kuti Fomu 4 ndiyo azilemba mayeso a boma. +Pofotokoza mmene zizidzayendera, nduna ya zamaphunziro, Dr Emmanuel Fabiano, idauza Tamvani kuti ndondomeko yatsopanoyi ikadzayamba bungwe la Maneb lidzasamba mmanja pachilichonse chokhudza JCE ndipo malo olemberamo mayeso (cluster centres) ndiwo adzasenze udindo. +Ndondomeko idzakhala yakuti malo olemberamo mayeso ndi ana omwe akuyenera kulemba mayeso azidzalipira ndalama za mayeso ku cluster yomwe izidzakonza mayeso ndi kulembetsa, adatero Fabiano. +Ndunayi idati sipadzakhala zobwereza kalasi kapena kuchotsedwaokhoza ndi olakwa omwe azidzapitirira mpaka mu Fomu 3. +Fabiano adati boma lagani izi pofuna kupereka mpata kwa ophunzira onse omaliza nawo maphunziro a kusekondale komwe akalemba mayeso a Fomu 4, okhoza azidzapatsidwa satifiketi ya MSCE pomwe olakwa azidzalandira kalata yaumboni yoti adamaliza maphunziro a kusekondale. +Iye adati izi zizichititsa kuti ambiri azilandira nawo maphunziro okwanira chifukwa mundondomeko yakale, olakwa JCE amachoka pasukulu ndipo ambiri sankakhalanso ndi chidwi chokapitiriza kwina. +Mfundo ya boma pochotsa mayeso a JCE ndi yakuti satifiketiyi idatha mphamvu chifukwa olemba ntchito ambiri masiku ano safuna satifiketiyi koma yokwererapo. +Ndege ya ufiti ikodwa ku Kasungu Ngakhale malamulo a dziko lino amakana kumutchula munthu kuti ndi mfiti, Amalawi ambiri amakhulupirira kuti ufitu uliko. +Anthu a mmudzi mwa Gundani mboma la Kasungu adodoma ataona chinthu chooneka ngati ndege chomwe akuchiganizira kuti ndi ndege ya afiti chitagwa mmudzimo. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Msangulutso utafufuza chomwe chidachitikita, udapeza kuti ndegeyo idagawa pakhomo pa Yusufu Abubaka Ali yemwe akukhulupilira kuti akola mfiti zomwe zakhala zikusautsa banja lawo. +Anthu amenewa adalodza akazi anga koma ndi mmene agwidwiramu akazi anga akhala bwino, adatero Ali. +Mkazi wa bamboyo Liness Kaulongo wakhala akudwala kwa nthawi yaitali ndipo kuchipatala cha boma ku Kasunguko adawauza akayesere zachikuda. +Tidapita kwa asinganga komwe adationetsa anthu anayi kuti ndi omwe akusautsa banja lathu. Singangayo adatipatsa mankhwala omwe adati tikaike panyumba yathu kuti ndidzakole mfiti zomwe zimanditambilazo, adatero Ali. +Iye adati sanadabwe kwambiri mkazi wake akuuza kuti kunja kwa nyumba yawo kwagwa chinthu chooneka ngati ndege. +Kaulongo, adati adadabwa kuona chinthu chamaonekadwe ngati ndege chili panja panyumba yayo pomwe adatuluka usiku kukataya madzi. +Mneneri wapolisi mboma la Kasungu Edwin Kaunda adatsimikiza kuti iwo akusungadi chinthu chomwe chikuganiziridwa kuti ndi ndege yaufiti. +Iye adati adapita pamalopo kukakhazikitsa bata chifukwa chinthucho chinkabweretsa mpungwepungwe pa malopo. +Ife tidapita kukatenga chinthucho ndipo tili nacho kuno kupolisi, adatero Kaunda. +ANATCHEZERA Mkazi wanga asabwere? Anatchereza, Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ndili ndi zaka 25 ndipo ndili pantchito yokhalira pomwepo. Ndine wokwatira ndipo ndili mwana mmodzi. Abwana anga aakazi ndi achikulire kwambiri ndithu koma ndikati ndiwapemphe kuti ndiitanitse mkazi wanga kuti tizidzakhala limodzi amakana. Ndichite bwanji pamenepa? Chonde, thandizeni maganizo. +I.J. +Mzuzu Zikomo IJ, Ndathokoza chifukwa cha kundilembera kuti ndikuthandizeni maganizo pankhani ya banja lanu. Kodi mudayamba mwawafunsa abwana anuwo kuti nchifukwa chiyani safuna kuti mkazi wanu abwere kuti muzikhala naye pantchitopo? Ndithu payenera kukhala chifukwa. Kodi abwana anuwo ali ndi amuna awo kapena ali okha? Ndafunsa dala mafunsowa chifukwa mwina akhoza kukuthandizani nokha kudziwa chifukwa chomwe safunira kuti mkazi wanu abwere pakhomopo. Mukandiyankha mafunsowa mwina ndidzatha kukuthandizani bwino pa chomwe mungachite chifukwa pano ndinama poti gwero lake lenileni lomwe amakanira kuti mkazi wanu abwere sindikulidziwa nkomwe. Ndisapupulume kupereka chigamulo pomwe nkhani yonse sindikuidziwa bwino lomwe. +Natchereza Sakundifunanso Gogo wanga, Ndidakwatiwa chaka chathachi pambuyo popanga chinkhoswe. Tidakhala mbanja mwezi wathuthunthu osandiuza kuti amamwa ma ARV koma tsiku lina ndidatulira nditapeza mankhwalawo mmabotolo. Nditamufunsa mwamuna wangayu adayankha kuti: Pepa mkazi wanga, ndimaopa kuti ndikakuuza ukana kuti tikwatirane. Koma usadandaule chifukwa ndisamala ana ako pamodzi ndi iweyo moyo wanga wonse. +Timakhalabe ngati banja, koma nditadwala ndidapita kuchipatala komwe adandiuza magazi koma amati zotsatira zake samaziona bwino. Nditapitanso adandiuza kuti ndilibe kachilombo ka HIV ndipo nditamuuza mwamuna wanga adati sakundifunanso banja ati chifukwa ndilibe kachilombo. Nditani? Chonde ndithandizeni. +Zina zikamachitika kumangothokoza Mulungu! Mwati mwamuna wanu akuti basi sakukufunaninso banja chifukwa mulibe kachilombo? Zoona? Cholinga chake kuchokera pachiyambi chidali chiyani? Kunena zoona, iyeyu adali ndi kampeni kakuthwa kumphasaamadziwa bwino lomwe kuti ali ndi kachilombo ka HIV ndipo ndikhoza kunena pano popanda mantha kuti cholinga chake chidali kufalitsa dala kachilomboko. Moyo woipa zedi umenewo. Kufalitsa dala kachilombo ka HIV kapena matenda ena alionse ndi mlandu waukulu ngati sindikulakwa ndipo munthu wotero ayenera kulangidwa. Ndiye inu mwati mwakayezetsa kawiri konse koma sadakupzeni ndi kachilombo, thokozani Chauta! Tsono ngati akuti sakukufunaninso ukwati, inu vuto lanu nchiyani? Alibe chikondi ameneyo, musiyeni mudakali moyo. Koma osangomusiyasiya ameneyo, mukamusumire kumabungwe kapena kukhoti kuti chilungamo chioneke mwina ena angatengerepo phunziro. +FAM ndi Kamuzu Stadium Sabata yatha kwathu kuno kudabwera alendo a Fifa kudzayendera bwalo la Kamuzu Stadium ngati ndi loyenera kuti mipikisano ya chikho cha World Cup iziseweredwapo. +Tidali ndi nkhawa kuti basi bwaloli alikana malinga ndi momwe likuonekera. Mukudziwanso paja kuti bwaloli lili ndi mavuto ambirimbiri. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Koma zidali zodabwitsa kumva akuti bwaloli lakhoza mayeso, kusonyeza kuti masewero a Malawi ndi Tanzania achitikira pomwepa. +Ife titapita kubwaloli, tidakapeza kuti a FAM akonza zingapo. Adasesapo komanso adakonza malo omenyera mapenote. +Alendowa, omwe adachokera ku Tunisia ndi Zambia, adangoona malo omenyera mapenote momwe akongolera. Kudzaonanso kuti zitsotso zonse asesa basitu adangoti choongu! Hahaha! Mpira ku Malawi sudzatheka. Boma lidakachitako manyazi abale. Izitu nzachisoni. +Bwaloli latha, tinene mosapsatira. Pena kukumakhala kulibe madzi moti aganyu akumadzithandizira mchikatoni. +Waya wa malire ndi posewerera adagwetsadwa kalekale moti masapota ataganiza zolowa mbwaloli mpira uli mkati angathe kuzichita ndipo zakhala zikuchitika. +Benchi ija idathyokathyoka ndipo adachita kubwerekera benchi ya ku Chiwembe kuti bwaloli likhoze mayeso. +Dziko lino lidakachitako manyazi, abale! Bwalo lija likupanga ndalama zambiri zomwe zikupita kuboma. +Boma litangonena kuti ndalama zopangidwa pa Kamuzu Stadium zisamapite mthumba la boma ndipo zithandizire kukonzera bwaloli, bwezi litakonzedwa kalekale. +Kudali ku mapemphero a Scom Patha zaka zisanu tsopano Dyson Milanzie yemwe ndi mkonzi wa mapologalamu kuwailesi ya kanema ku MBC-TV ali pabanja ndi njole yake Jane. +Awiriwatu adamangitsa woyera pa 30 July 2011 ku Word Alive Garden mumzinda wa Blantyre. +Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Adakumana ku BSS: Dyson ndi Jane Dyson amakhulupirira kuti Mulungu ndiye adagwira ntchito yonse kuti iwo akumane ndi kumanga woyera. +Iwo adadziwana mchaka cha 2003 pomwe Jane amaphunzira kusukulu ya sekondale ya Blantyre (BSS), Dyson ali kusukulu ya pulaiveti ya Kamacha koma onse nkuti ali Fomu 2. +Mchakachi sukulu ya Dyson idakonza mapemphero a Students Christian Organization Malawi (Scom) omwe amakachitikira ku sukulu ya BSS. Kupatula mapemphero, Dyson adagwiritsira ntchito nzeru zachibadwidwe pamene adaponya maso pa Jane. +Macheza okhudza mapemphero adayambira pomwepo, koma mosakhalitsa zinthu zidasintha, Dyson adaganiza zolankhula nkhani ina kwa njoleyi ndipo mu 2004 Dyson adafunsira njoleyi koma tsoka ilo adakana. +Izi akuti zidabalalitsa Dyson chifukwa maso ake amalasalasa pa njoleyi kotero kudali kovuta kuti ayangane kwina. +Mnyamatayu sadalekere pomwepo, adayeserabe kuponya Chichewa chake ngakhale chimakanidwa koma mu 2005 pamene njoleyi imaphunzira pa koleji ya Polytechnic, akuti mpomwe idalola Chichewa cha Dyson. +Jane akuti loto lake lidali lodzagwa mchikondi ndi mwamuna wokhulupirira Mulungu. Iye akuti ataonanso kuti kupemphera kwa Dyson sikudali kwachinyengo, adaganiza zomulola. +Kukhulupirira Mulungu akuti ndicho chakhala chinsinsi chawo kuti lero angakwanitse zaka zisanu popamba kuponyerana mapoto kapena kuitana ankhoswe kuti adzaweluze milandu. +Awiriwa ati achinyamata azizisunga ngati akufuna kudzagwa mmanja a munthu woopa Mulungu. +Dyson Milanzie ndi wa mmudzi mwa CheMgundo kwa T/A Kumtaja mboma la Blantyre ndipo ndi wa 9 mbanja la ana 11. +Atudzula ziwalo za mwamuna wake Pamene nkhanza zambiri zomwe zimachita zimakhakla zochokera kwa abambo kupita kwa amayi, Loveness Nakayuni wa mmudzi mwa Chapyoka, T/A Mwaulambia mboma la Chitipa, masiku apitawa adali mchitolokosi pomuganizira kuti adafinya mwamuna wake kumalo obisika mpaka kutudzula ziwalo. +Mneneri wa polisi mchigawo cha kumpoto Maurice Chapola adatsimikiza za nkhaniyi pouza Msangulutso kuti mayiyo adali mmanja mwawo kaamba kovulaza mwamuna wake, Winis Kita, wa zaka 46, atamugwira kumoyo chifukwa akuti adaphwanya lonjezo logona kunyumba kwake. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Iye adati Kita, yemwe ndi wamitala, adanyamuka kupita kukamwa mowa komwe adabwerako madzulo. +Iye adafikira kunyumba kwa mkazi wake woyamba, Nakayuni, koma sadakhalitse ndipo adapita kunyumba ya mkazi wake wamngono. Izi zidamuwawa Nakayuni, yemwe adamulondola mwamunayo kunyumba kwa mkazi wake wamngonoyo. +Atafika adapeza mwamunayo atakhala pakhonde akusuta fodya. Nakayuni adangombwandira malo obisika a mwamuna wakeyo nkufinya mpaka kutudzula, adafotokoza Chapola. +Iye adati Kita adamutengera kuchipatala cha boma komwe adalandira thandizo lobwezeretsa ziwalozo zake mchimake. Pano akuti akupezako bwino ndipo akuchita kuyendera kukalandira mankhwala kuchipatala. +Funso nkumati kodi banja lilipobe apa? Tidalephera kuyankhula ndi Kita, koma wapolisi wa zofufuzafufuza, teketivu Yatamu Kasambara, adauza Msangulutso kuti mkuluyu adakatseketsa mlandu kupolisiko ponena kuti zidali zambanja ndipo mkazi wake pano ali kunyumba ati azikalera ana. +Ku Chitipa komweko, mayi wina, Mawazo Nzunga, akumuganizira kuti wapha mlamu wake atamumenya ndi mpini wa khasu pamutu atalephera kumvetsetsana pankhani ya chakudya. +Chapola adauza Msangulutso kuti wophedwayo, Willard Mwilenga, adapita komwa mowa ndipo pochoka kumowako adaganiza zokapempha chakudya kunyumba ya mbale wake komwe adauzidwa kuti chakudya chake kulibe. +Yankho la mlamu wakeyo silidamusangalatse ndipo kaamba ka kuledzera adayamba kummenya. Nzunga pobwezera adatenga mpini wa khasu ndipo adamugogoda nawo pamutu nkumukomola nawo, adafotokoza Chapola. +Mwilenga adathamangira naye kuchitapatala cha Kameme koma ataona kuti zawakulira adamutumiza kuchipatala chachikulu ku Chitipa komwe adakafera. +Chapola adati Nzunga ali pa rimandi pandende ya Chitipa kudikira kuyankha mlandu wa kupha munthu. +Pothirapo ndemanga pankhani za nkhanza, wapampando wa bungwe la NGO Gender Coordination Network, Emma Kaliya, wati nkhani kuti itengedwe kuti ndi ya nkhaza kwa amayi kapena abambo zimakhala bwino kuyangana chatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke mnyanga. +Mboma la Chitipa amuna ndi azikazi awo ali ndi kachisimo kokamwa mowa ku chilabu limodzi, makamaka madera a kwa Kameme ndi Mwaulambia. +Tikuyesetsa kuthana ndi mchitidwe womwa mowa ku chilabu chifukwa tikukhulupirira kuti umakolezera nkhaza pakati pa amayi ndi abambo, adatero Kaliya. +Kulira kwanyanya mzipatala Kubangula ndi kulira mokweza kukumveka mzipatala za mdziko muno pomwe boma lachepetsa ndalama zopita kuntchito za chipatala potsatira mavuto a zachuma amene dziko lino likukumana nawo. +Mneneri wa unduna wa zaumoyo Adrian Chikumbe wavomereza za vutoli ndipo adati undunawo udalandira ndalama zochepa kuchokera ku nthambi ya za chuma. +Chisale watuluka nkumangidwanso Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Odwala akuona masautso mzipatala Tikuyesetsa kuti tipeze ndalama zoonjezera ndipo pakadalipano tikuyankhula ndi mabungwe omwe angatithandize, adatero Chikumbe. +Iye adati akuyembekezera kuti ayankhidwa mwezi uno kapena miyezi iwiri ikubwerayi. +Zipatala zachepetsa ntchito zambiri makamaka mayendedwe a maambulansi komanso chakudya chikumaperekedwa kamodzi kapena kawiri patsiku mmalo mwa katatu. +Dokotala pa chipatala cha Karonga Charles Sungani adauza Tamvani kuti achepetsa chakudya cha odwala kuchokera pa kudya katatu kufikira pa kawiri patsiku. +Ambulansi nazo mafuta zilibe ndipo pakadali pano maambulansi akumangogwiritsidwa ntchito kunyamula amayi oyembekezera omwe ali ndi mavuto, adatero Sungani. +Iye adati pofika sabata ya mawa mafuta amene ali nawo akhala atatha. +Mmaboma a Mzimba ndi Nkhata Bay odwala akumadya chakudya kamodzi patsiku ndipo ambulasi zambiri zikungokhala kaamba ka kusowa kwa mafuta kuti galimotozo ziziyenda. +Dokotala wamkulu mboma la Nkhata Bay Albert Mkandawire adadandaula kuti ndalama yomwe adalandira ndi yochepa kwambiri kuti ithandizire zipatala zonse mbomalo. +Talandira K4.8 miliyoni yomwe ikuyenera kupita ku zipatala zoposa 20. Ndalama imeneyi ndi yochepa kwambiri kuti itithandize pantchito za pachipatala, adatero Mkandawire. +Ngakhale zinthu zili choncho mmaboma ena, monga la Dedza, sadalimve kuwawa kwambiri vutoli chifukwa aphungu a Nyumba ya Malamulo awo adagwirana manja ndi kuthandizapo. +Mneneri wa chipatala cha Dedza, Arnold Mndalira, adati achipatala adawauza aphunguwo za kuchepa kwa ndalama zomwe zidabwera kuchoka kuboma. +Mndalira adati apa aphunguwo adasonkherana limodzilimodzi ndi kuonjezera ndalama pachipatalapo. +Adapereka K2.4 miliyoni yomwe theka lidapita ku chakudya ndipo theka lina lidapita ku mafuta a galimoto, iye adatero. +Ntchito iyamba September uno Boma liyamba kuthandiza okhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi Boma lati ntchito yokonza zinthu zomwe zidawonongeka ndi chigumula cha madzi osefukira kumayambiriro kwa chaka chino iyamba posachedwa. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mneneri wa unduna wa zachuma Nations Msowoya adatsimikiza Lachitatu lapitali pocheza ndi Tamvani kuti ntchitoyi, yomwe ikuyembekezeka kugwiridwa mmagawo awiri, iyamba mwezi wa September chaka chino. +Msowoya adati ndalama zomwe zilipo nzochepa kuyerekeza ndi zomwe zikufunika koma adati ntchitoyo iyambabe pofuna kupereka mpata wopezera ndalama zina zotsalirazo. +Pali ndalama zomwe zichokere kubanki yaikulu ya World Bank zokwana K41.6 biliyoni ($80 miliyoni) komanso boma mundondomeko ya chuma cha 2015/2016 lidakhazikitsa thumba la ndalama zogwirira ntchito yomweyi koma sizikufika pa ndalama zomwe zikufunikazo. +Poti awa ndi mavuto ogwa mwadzidzidzi sitingadikire kuti ndalamazo zipezeke zonse, ayi, tiyambapo kugwira ntchito zinazo zikamapezeka tiziona kuti zipite pati mpakana titamaliza kukonza zonse, adatero Msowoya. +Iye adati zokonzekera zonse zidayamba kale ndipo kuyambira mwezi wamawawu ntchitoyo iyambika potengera zinthu zofunikira kwambiri. +Msowoya adati ndime yoyambirira ikhala yotukula miyoyo ya anthu powaganizira ndi zipangizo monga zaulimi zomwe azilandira akagwira ntchito ya chitukuko mmadera momwe mudakhudzidwa kwambiri ndi madzi osefukirawo. +Bernard Sande, woyendetsa ntchito zolimbana ndi ngozi zodza mwadzidzidzi, adauza Tamvani Lachiwiri kuti ntchito yonse yokonza zinthu zomwe zidawonongeka pangoziyi ikufunika ndalama zokwana K215 biliyoni. +Sande adati nthambi yoona za ngozi zadzidzidzi idachita kafukufuku wa zinthu zomwe zidaonongeka ndipo idapeza kuti zinthu za ndalama zokwana K146 biliyoni ndizo zidakhudzidwa. +Tidachita kafukufuku wokwanira ndipo tidapeza zambiri zomwe zidaonongeka zofunika kukonzanso pomwe zina nzofunika kugula ndi kubwezeretsa. Tikudziwa kuti ndi ntchito yaikulu, koma boma lidatilimbitsa mtima kuti zitheka, adatero Sande. +Gift Mafuleka, yemwe ndi wachiwiri kwa woyendetsa ntchito zothana ndi mavuto ogwa mwadzidzidzi, adati anthu oposa 900, 000 ndiwo adakhudzidwa ndi madzi osefukira mmaboma 15 pa maboma 28 a mdziko muno. +Adanena izi litatuluka lipoti loyamba lokhudza momwe chigumulacho chidawonongera potengera malipoti a mmaboma omwe adakhudzidwa. +Mafuleka adati ambiri mwa anthuwa akusoweka zipangizo zomangira pokhala, madzi aukhondo, ziwiya, chakudya ndi zina. +Iye adati mmadera ena okhudzidwawo mudaonongeka nyumba za ogwira ntchito mboma monga aphunzitsi, komanso nyumba za sukulu zomwe zikufunika kukonzedwa kuti zizigwira ntchito yake. +Chachikulu kwambiri anthu okhudzidwawo akufunika zipangizo zomangira pokhala chifukwa ena mwa iwo akukhalabe mmisasa monga msukulu, ndiye tili ndi nkhawa chifukwa sukuluzo zikufunika zizigwira ntchito [yophunzitsirako ana], adatero Mafuleka. +Yamikani Headmaster Fodya wa Bullets Dzina la Yamikani Fodya lawanda. Uyutu ndi mnyamata wokankha chikopa kutimu ya Flames komanso ku Big Bullets. Iyeyu wapatsidwa maina osiyanasiyana kaamba ka luso lake lomwe ochemerera mpira akuliyamikira monga mwa dzina lake. BOBBY KABANGO akumva za mbiri yake. +Fodya: Mulungu akakonza palibe angatsutse Tikambire za mbiri yako Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ndimachokera ku Balaka. Ndine wa nambala 7 kubadwa mbanja la ana 8. Ndinenso wokwatira ndipo ndili ndi mwana mmodzi dzina lake Favour. +Ku Bullets udabwerako liti? Ndidafika mumzinda wa Blantyre mu 2009. Nthawiyo nkuti kutangoyambika chikho cha Presidential Cup ndiye anthu adaona luso langa mpaka kundiitanira kutimuyi. +Udalandiridwa bwanji? Kundirandira kudali bwino koma kupeza mwayi wosewera padavuta. Ndidapeza osewera ambiri, ngakhale ku training sindimapeza mwayi. Ngakhale kutulutsa timu yonseyo, mwayi wolowabe sumapezeka. +Nanga umasewera malo ati? Nthawiyo ndimasewera pakati, malo amene ndimasewera ku Young Soccer ya ku Dedza. +Zidatani kuti uyambe kusewera kumbuyo? Idangokhala pulani ya Mulungu chifukwa kochi wa timuyi panthawiyo, Meke Mwase, adandifunsa za malo amene ndimasewera ndiye ndidangoti kumbuyo. Basitu kuyamba kusewera kudali komweko. +Zidayamba kukuyendera mchaka chanji? Mu 2010. Chaka chimenechi ndidasankhidwanso wosewera amene wachita bwino kumbuyo. Koma kuchoka nthawiyo mpaka 2013 ndiye zidavuta chifukwa ndidavulala msana. +Wafala paliponse ndi luso lako, kodi ndi mankhwala? Mbale wanga, Mulungu akakonza palibe amene angatsutse. Pamene sizimayenda ndimalimbikirabe kuti tsiku lina zidzayende. Palibe mankhwala koma mphamvu yake basi. Si nzeru zanga koma chifundo chake cha Mulungu. +Malo amene ukusewera ku Flames umalimbirana ndi Francis Mlimbika, kodi simuchitirana nsanje? Francis ndi mbale wanga, ndimamupatsa ulemu ndipo ndimakondwera naye. Dziwani kuti nayenso Mulungu adamupatsa luso. Ngati lusolo lili la Mulungu, ine ndani kuti ndimuchitire nsanje? Kodi ukungotchula za Mulungu bwanji? Uli mpingo wanji? Mbale wanga, palibe munthu amene sadziwa kuti kumwamba kuli Mulungu. Ngakhale wakuba amadziwa. Tili mmasiku omaliza, palibe chomwe tingachite ngati iye palibe. Malembo amati ngati Iye samanga nyumba omangayo amanga pachabe. Nchifukwanso ndimatsogoza Mulungu pazonse. Ndikupemphera mpingo wa Seventh Day Adventist. +Ukutchulidwa maina osiyanasiyana, kodi mainawa adabwera bwanji? Tili ku Cosafa, onenerera mpira amanditchula kuti Soul Brother ati chifukwa cha tsitsi langali limafanana ndi oimba a gulu la Soul Brothers kumeneko. Kunoko anthu andipatsa dzina loti Headmaster chifukwa ndimapisira malaya 90 minitsi. +Kodi sumeta chifukwa chiyani? Nanga kupisiraku? Ndimasangalala ndi osewera mpira akale amene samameta wamba, mametedwe alerowa kudalibe. Komanso amapisira ngakhale ma jersey ndi makabudula awo adali aangono. Zimenezi zimandisangalatsa. Komanso ndimamukumbukira Chisomo Kamulanje amene adandiuza zambiri za malo amene ndimasewera aja. Pamene amachoka ku Bullets ndidanena kuti ndikufuna ndidzapange chinthu chomwe ndidzamukumbukire nacho. +Fodya nkunazale Pamene alimi a fodya ali yakaliyakali kukonzekera ulimi wa 2015/16, mlangizi wa zaulimi wa fodya mboma la Rumphi, Charles Jere, walangiza alimi kuti atsatire ndondomeko ndi malangizo oyenera popanga nazale ya fodya pofuna kupindula ndi ulimi wawo. +Pocheza ndi Uchikumbe posachedwapa, Jere adati nazale ya fodya si ili ngati ya ndiwo zamasamba kaamba koti imafuna chisamaliro chapadera chifukwa kupanda kutero palibe chimene mlimi wa fodya angapindule ndi fodya nchifukwa chake pali mawu akuti fodya nkunazale. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Choyamba mlimi akuyenera kupeza malo omwe aikepo nazale yake. Malowa akuyenera kukhala kufupi ndi madzi oyenda kapena omwe akuoneka opanda tizilombo toyambitsa matenda a mtundu wina ulionse, adatero Jere. +Jere adati mlimi akuyenera kutipula nazale kutengera ndi kukula kwa munda wake. Mlangiziyu adati paekala imodzi bedi la nazale likuyenera kukhala lotalika mamita 30 ndi mita imodzi mlifupi pomwe hekitala imafunika mabedi atatu a muyezo woterewu. +Akapanga bedi lija mlimi akuyenera kutenga mapesi a chimanga nkuwasanja pabedi lija ndipo akatero awaotche ndi cholinga chofuna kupha tizilombo tomwe tidali mudothi tomwe tikadatha kuononga fodya panazalepo. +Apa adikire masiku awiri kapena atatu kuti ayambe kufesa fodya panazalepo, adafotokoza Jere. +Iye adati mlimi ayenera kuthira feteleza wokwana makilogalamu atatu asadafese fodya uja. Akafesa fodyayo athire mankhwala kuti aphe tizilombo monga nyerere zomwe zikhoza kudya mbewuyo. +Mankhwala ena ofunika kuthira panazale ndi amene amapha tizilombo toyambitsa matenda ena mufodya, adatero Jere. +Malinga ndi Jere, mankhwalawa amafunika kusungunula mutheka la madzi a mukheni ndi kuwathira panazale paja pataikidwa kale maudzu. +Njoka zoweta ndi penshoni Pa Wenela tsikulo padafika nganga ina imene inkati yangofika kumene kuchokera ku Mozambique, inde dziko la nkhondo. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ngangayo idafika ndi chikwama chake chasaka momwe idatulutsa njoka zingapomphiri, nsato, mbobo, nalikukuti, mamba ngakhalenso chilere, njoka yopanda ululu. +Ankafanana ndithu ndi Moya Pete. Kulankhula, chimodzimodzi. +Ku Tete ndabwerako. Ndathawa nkhondo kwambiri. Ndabwera ndi njoka zoweta, adatero mkuluyo. +Akulu, njoka yoweta sagula pamsika, nanjinanji wa ku Mozambique! adatero Abiti Patuma. +Ukunama kwambiri. Izi ndi njoka zowetedwa nthawi ya Machel, Chissano, Guebuzza ndi uyu winayu. Kaya mukuti ndani uyu. Mwana wa ndani uyu, adatero singanga uja. +Abale anzanga, tidaona zozizwitsa. Njoka imodzi idayangata mwendo wake nkulowa mkabudula mwake nkutulukira kwinako, nkukazinga mutu wake. Ina idachoka paphewa, kulowa mkabudula, nkukazinga mwendo. Njoka saweta. +Akulu, kodi njokazi mukufuna mutikawe, kapena chiyani? adafunsa Abiti Patuma. +Adakuuzani kuti njoka saweta adakunamizani kwambiri. Izi ife a namanyonyoro timaweta kwambiri kwathu ku Cholo, adatero singanga. +Nkhani ili mkamwa adatulukira Shati Choyamba. +Mkulu iwe, ulipo? Kodi paja unkafuna kupha gogo wina ndi cholembera, zikuyenda bwanji? Nanga paja udalamulira pano pa Wenela nthawi ija gogo wathu akudwala, ndalama za penshoni udatani nazo? adafunsa Abiti Patuma. +Usandiseke. Maluzi andikwapula. Ana anga sakundithandiza mokwanira. Chonde pano pa Wenela musanyoze achikulire, adayankha mkulu wa imvi zaphulusayo. +Umufune! Kodi suja unkamuuza Mfumu Mose kuti sungayendere galimoto yotchipa kuposa BMW X5? Si iwe, ndiyankhe, adatero Abiti Patuma. +Komatu muzimvetsetsa. Ndili kukhala mu boys quarter pafupi ndi damu la anamasupuni ku Chimwankhunda, adatero mkulu uja. +Kodi ndalama za penshoni sudamange nyumba? Nanga zotsogolera kutsutsa mopusa? Nanga za mapesi unkationetsa zija? Ukakamba za nyumba, ija ili pafupi ndi mtsinje njira ya ku East Bank? ndidafunsa. +Adandiyangana kenaka adati: Ndalama za penshoni samangira nyumbatu paja! Gwira bango, upita madzi. +Moya Pete wagwa nayo Abale anzanga, lero palibe kucheza pa Wenela. Musandifunsenso kuti chifukwa chiyani chifukwa sindingakuuzeni. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Kodi simukudziwa kuti zinziri zinalowa pachipatala choyandikira pa Wenela? Abiti Patuma ndiye adandiuza kuti zibakera zinavuta mu Chilekamu mpaka ena kugonekedwa mchipatala. +Kaya ndewuyo inali ya mbanja, kaya zachibwenzi koma kudali kusinjana ngati wina wagundidwa ndi sitima kuseri kwa Wenela. +Koma amukwapula. Ena akuti mpaka mutu sukugwira ntchito mpaka kuthawa kuchipatala. Zovuta, adatero Abiti Patuma tsikulo. +Koma nsakutayitseni nthawi ndi zokamba za Abiti Patuma. Chifukwatu iyeyo ndi mnzake wa Mori wokunthidwayo. Komanso uyu Marison wokunthayo ndi mnzake ndithu. Iyetu adaphunzitsa ambiri kuti mowa sukuyenera kulepheretsa munthu sukulu komanso sukulu isalepheretse munthu mowa. +Tsonotu lero sikuti pali zonena za pano pa Wenela chifukwa ndatopa nazo. Ndalema. Ndikudabwa. Kodi mukuti kuli Moya Pete? Abale anzanga, nkadakhala mkuluyu nkadasiya zonse. +Sizikuyenda. Magetsi kulibe. Madzi nawo ndi anjomba. Kunena za kuchipatala, mankhwalanso kulibe. +Lero akuti tizidya kamodzi tikakhala ku Wodi 3B. Eti ngati tili kundende. +Mkulu zamulaka. Walephera. Sanakhoze. +Titambasule za madzi. Nanga lero munthu nkumanena kuti ndi bwino kumwa madzi pachitsime? Lero lino kutunga madzi padilawo nkukhala munthu wolemekezeka? Walephera. Apondeponde akaone zina ku America kuli ana akeko. +Nanga lero munthu nkumakamba za koloboyi, ati madzi achepa mu Shire? Dzulo ndi dzana adatiuza kuti madzi achuluka zedi moti sangathe kutapa magetsi. Lero akutinji? Walephera. +Nanga taonani umu akudulira mitengo! Ngakhale muwauze alonda a nkhalango akhale ndi mfuti, ateteza chiyani? Mitengo idatha. +Walephera. +Kunena za malata, simenti ndi zina zija adalonjeza kuti adzatsitsa, zakwera mtengo chifukwa ndalama yake akulephera kuigwira. +Walephera. +Nanga tinene za mpira wa zikhatho, inde mpira wa mafumukazi! Nanga kulephera tinene kuti nkukhoza? Kuchinyidwa tinene kuti nkuwina? Walephera mwana akagone. +Sindinganenenso za uchifwamba chifukwa uko ndiye wagwa nayo zedi. Walephereratu. +Zilo pa 10. +Walephera mwana akagone. +Kumaphunziro sinditaya nako nthawi. Kungotsegulira Poly, anyamata ali pamsewu. +Walepheranso. +Nanga chilungamo? Alibe chilungamo. Wakuba ana, ati akakhale kumalo aja ozizira zakaziwiri. Mbali inayi, wokwapula mkazi wake, ati akakhale pashamba zaka 13 ndi theka. +Walephera ndithu. +Zisiye iwe. +Gayighaye Mfune: Wosula oimba Kuimba ndi luso lomwe ena amabadwa nalo pomwe ena amachita kuphunzira. Maphunziro a zoimbaimba amachuluka zifanifani ndipo zimatengera luso la mphunzitsi kumasulira zifanifanizo kuti ophunzira amve. Mathews Gayighaye Mfune ndi mmodzi mwa akatakwe ophunzitsa zoimbaimba ndipo amayendetsa sukulu ya zoimba ya Music Crossroads Malawi. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere: Tidziwane, akulu. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Mfune: Ndimafuna kuti oimba apite patali Ine ndine Mathews Gayighayi Mfune ndipo ndimachokera mmudzi mwa Chipofya kwa T/A Katumbi mboma la Rumphi. Ndili ndi digiri ya zamaphunziro yomwe ndidatenga ku University of Malawi. Ndidapanganso dipuloma ya zachikhalidwe ku South Africa. Ndidagwirapo ntchito ku unduna wa zamasewero ndi chikhalidwe ndipo pano ndikuyendetsa sukulu ya zoimbaimba ya Music Crossroads Malawi. +Mumawoneka kuti muli ndi luso la zoimbaimba, kodi mudaphunzira kuti? Kuimba ndi mbali ya chibadwa changa komanso ndidazolowera kucheza ndi oimba, otukula oimba ndi ojambula nyimbo ku Malawi kuno komanso mmaiko akunja. Kuunduna wa zamaswero ndi chikhalidwe, ndinkayendetsa za luso loimba ndi zisudzo komanso maphunziro omwe ndidachita ku South Africa adandiika patali kwambiri. +Tandiuzeni mbiri ya Music Crossroads. +Limeneli ndi bungwe lomwe si laboma komanso si bizinesi ayi. Lidakhazikitsidwa mchaka cha 2007 kuti liziphunzitsa achinyamata zoimbaimba. Bungweli limaphunzitsa oyimba oposa 500 pa luso loimba kudzera mmipikisano ndi maphunziro a tsiku ndi tsiku. Kupatula kuphunzitsa achinyamata kuimba, timaphunzitsanso akaidi za matenda a Edzi, kuimba, kujambula ndi kupanga zimbale. Mwachidule ndife nthambi ya Jeunnesses Musicale International (JMI). +Masomphenya anu pa nkani yoimba muno mMalawi ndi otani? Ndimafunitsitsa kuti oimba athu adzafike patali ngati oimba a mmaiko ena komanso anthu adzayambe kuzindikira kuti kuimba ndi ntchito yandalama zambiri kuti adzakhale ndi ludzu lotukula zoimbaimba. +Bungwe lilimbikitsa ulimi wa akalulu Akalulu ndi mtundu wa ziweto zingonozingono zomwe alimi ambiri amanyalanyaza kuweta koma katswiri paulimi wa ziweto zosiyanasiyana, Sute Mwakasungula, wati ulimiwu ndi wopindulitsa. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Mwakasungula, yemwe ndi mkulu wa bungwe lomwe limagwira ntchito ndi alimi a ziweto aangono la Small Scale Livestock and Livelihoods Programme (SSLLP) akuti ulimi wa akalulu suboola mthumba ndipo uli ndi ubwino wochuluka. +Muli chuma: Akalulu savuta kudyetsa Kupatula kuchita ndiwo pakhomo, mkuluyu adati akalulu amabweretsa ndalama komanso mlimi amapindula ndi manyowa ochokera mkhola la akalulu ngakhale kuti iye amalowetsa ndalama zochepa. +Choyamba, akalulu savuta kudyetsa chifukwa amadya zopezeka mosavuta. +Kusamala kwakenso, monga kumanga khola ngakhalenso kunyamula nkosavuta chifukwa cha msinkhu wake, adatero Mwakasungula. +Iye adati chisamaliro chakathithi ndiye chinsinsi cha phindu paulimi wa akalulu chifukwa kulephera kutero, akalulu amagwidwa matenda kapena kujiwa ndi zinyama zolusa. +Khola la akalulu limafunika kukhala labwino. Akalulu amafuna chitetezo chachikulu kunyengo monga dzuwa, mvula ndi kuzizira. +Amafunikanso chitetezo kunyama zolusa monga njoka, agalu, afisi ngakhalenso makoswe. Komanso safuna kusokonezedwa ndi phokoso, adatero Mwakasungula. +Iye adati mbewu ya akalulu imapezeka mosavuta mmalo a zaulimi monga kusukulu ya ukachenjede ya Bunda, nthambi za boma zokhudzidwa ndi ulangizi wa zaulimi ngakhalenso alimi ena a akalulu. +Mwakasungula adati nkhani ina yaikulu pa ulimiwu yagona pa katetezedwe kumatenda, makamaka pokhala tcheru nthawi yosankha akalulu oweta. +Nthawi zonse mlimi ayenera kuonetsetsa kuti akalulu sakuchucha mmphuno, alibe zilonda mmakutu, kumapazi ndi malo obisika. Mwachidule, pogula akalulu oweta, gulani komwe muli nako chikhulupiriro kuti kulibe matenda, adatero Mwakasungula. +Mkuluyu adati madzi ndi ofunika kwambiri pankhani yodyetsera akalulu mwakuti mkhola mumayenera kukhala madzi nthawi zonse chifukwa kalulu mmodzi ndi ana ake amamwa malita awiri patsiku. +Iye adaonjeza kuti pali zakudya zina zosayenera kudyetsa akalulu monga zakudya zomwe zaunga ndere, masamba a mbatatesi, masamba a mabilinganya ndi masamba a chinangwa. +Mwakasungula adati pofuna kusintha chakudya cha akalulu, pamafunika kusintha pangonopangono osangoti kamodzinkamodzi modzidzimutsa chifukwa kuteroko kumasokoneza mmimba mwa akalulu ndipo akhoza kudwala nkufa. +Zavutanso ku Mozambique Othawa nkhondo ayamba kufika mdziko muno Zavutanso ku Mozambique. Nkhondo ya pachiweniweni pakati pa otsatira chipani cholamula cha Frelimo ndi chotsutsa cha Renamo yagundikanso ndipo nzika zina za mdzikomo zayamba kuthawa nkhondo kukhamukira mdziko muno pofuna kupulumutsa miyoyo yawo. +Koma ngakhale izi zili choncho, mtendere sadaupezebe. Ambiri akugona kumimba kuli pepuu, alibe zovala, zofunda komanso pokhala. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Umu ndi momwe zilili mmudzi mwa Kapise kwa Senior Chief Nthache mboma la Mwanza komwe kwaunjikana nzika za dzikolo. +DC wa bomali, Gift Rapozo, watsimikiza kuti zawathina masamalidwe a nzikazo chifukwa kuofesi kwawo kulibe chakudya komanso matenti oti asamalire anthuwa pamsasa pomwe afikirapo. +Zikatere maso amakhalano kuboma kuti litithandize ndi chakudya komanso malo oti anthuwa akasungidwe. Ife ndiye tagwira njakata chifukwa tilibe chakudya, adatero Rapozo polankhula ndi Tamvani kumayambiriro a sabatayi. +Othawa nkhondowa akuti adayamba kufika mdziko muno pa 5 July ndipo pofika Lolemba lapitali nkuti anthu 678 atafika mmudzi mwa Kapise. +Mdziko la Mozambique mudabuka nkhondo ya pachiweniweni mchaka cha 1977 patangopita zaka ziwiri chithereni nkhondo yomenyera ufulu wa dzikolo mchaka cha 1975. +Nkhondo ya pachiweniweniyo idatha mu 1992 ndipo chisankho choyamba cha matipate chidachitika mu 1994. Chipani cha Frelimo ndicho chidapambana. +Malinga ndi kafukufku wathu pa Intaneti, mmene nkhondoyo imatha nkuti anthu 1 miliyoni atataya miyoyo yawo pophedwa ndi asirikali a boma komanso zigawenga za Renamo, kunyentchera ndi matenda ena osiyanasiya monga malungo, kamwazi, likodzo ndi khate. Ena 500 000 adalibe pokhala komanso anthu 5 miliyoni adali atathawira maiko ena kuti akapeze mpumulo. +Dziko la Malawi ndilo linkasunga othawa nkhondo a ku Mozambique oposa maiko ena onse oyandikana nawoanthu osachepera 1 miliyoni adasungidwa kumisasa mmaboma a Nsanje, Chikwawa, Mwanza ndi maboma ena. Ku Nsanje kokha kudali nzika za ku Mozambique 200 000, kuposa chiwerengero cha eni nthaka mbomalo. +Ngakhale dziko la Malawi lidali pamavuto aakulu a zachuma ndi kuonngeka kwa chilengedwe kaamba kosunga othawa kwawowa, lidachitabe chamuna kuonetsa umunthu powapatsa zithandizo zosiyanasiyana kuti ayiwale kwawo, zomwe zidasangalatsa bungwe la United Nations ndinso maiko ena akunja. +Chodabwitsa nchoti pankhondo ya pachiweniweniyo, boma la Malawi, pansi pa ulamuliro wa pulezidenti wakale, malemu Dr Hastings Kamuzu Banda, linkathandizira mbali zonse za Frelimo ndi Renamo. +Posafuna kuonetsa kukondera, mwamseri Kamuzu ankagwiritsa ntchito Apayoniya (Malawi Young Pioneers) kuthandizira Renamo pomwe ankatumiza asirikali ankhondo a Malawi Army kuthandizira Frelimo pofuna kuteteza katundu wa boma la Malawi amene ankadzera mdzikolo. +Bata ndi mtendere zidayamba kukhazikika mdzikomo koma pofika mchaka cha 2013 ziwawa zidayambiranso ndipo mpaka lero mtendere weniweni ukusowekera moti kumenyana pakati pa otsatira zipani za Frelimo ndi Renamo kwabukanso. +Anthu mdzikomo akhala akupempha mtsogoleri wawo, Filipe Nyusi, yemwe wangotha miyezi 6 chilowereni mboma, kuti achite machawi pokambirana ndi Afonso Dhlakama, mtsogoleri wa Renamo, pofuna kuthetsa kusagwirizanako. +Msabatayi, Nyusi adauza nyumba zofalitsa nkhani mdzikomo kuti achita chotheka kukambirana ndi Dhlakama pofuna kukhazikitsa bata mdzikomo. +Kusamvana kwa mbalizi kwachititsa kuti anthu wamba, maka amene akukhala ku Mkondezi, malo amene achita malire ndi dziko lino, akhale akapolo pamene akuwayatsira nyumba komanso kuphedwa, zomwe zachititsa kuti ena athawe mdzikomo ndi kukabisala mmaiko oyandikananawo monga Malawi. +Komabe kusamala anthuwa kukuoneka kuti kukhala kovuta kudziko la Malawi lomwe kumayambiriro a chaka chino lidali ndi mavuto a kusefukira kwa madzi lomwe lidachititsa kuti anthu alephere kukolola chakudya chokwanira. +Chipani cha Renamo chimakana kuti chidagonja mchisankho cha mu 2014 zomwe zachititsa kuti zipani ziwirizi zikhale pachimkulirano. +Kaamba ka izi, Dhlakama wakhala akuopseza kuti ayambiranso kuchita mtopola womwe ubutse nkhondo mdzikomo pokhapokha dandaulo la chipani chake litamveka. +Usiku wa Loweruka lathali, Dhlakama adauza nyumba ina youlutsira mawu mdzikomo kuti asirikali ankhondo okwana 53 aphedwa kale chiyambireni mwezi wa June. +Kelvin Sentala wa bungwe la United Nations High Commissioner for Refugees (UNHCR) wati bungwe lawo likudziwa kuti anthuwa alowa mdziko muno, koma adakana kufotokoza zambiri ponena kuti mneneri wawo, Monique Ekoko, yemwe foni yake simayankhidwa, ndiye angalankhulepo. +Nduna yoona za mdziko, Atupele Muluzi, sadayankhe foni yake kangapo konse Tamvani idayesera kumuimbira. +Msika wa osewera watentha Pamene matimu ali kopumira kukonzekera ndime yachiwiri ya 2015 TNM Super League, msika wa osewera wafika potentha pamene matimu ali kalikiriki kugula ndi kugulitsa osewera ncholinga chofuna kuchita bwino mligiyi ikayamba mndime yachiwiri. +Tiyamba ndi timu yomwe ikuteteza ligiyi yomwenso ikutsogola ndi mapointi 32. Iyi ndi Big Bullets, yomwe padakalipano ikukambirana ndi timu ya Mzuni FC kuti itenge mnyamata womwetsa zigoli wa ku Burundi, Aimable Niyikiza, amene tikukamba pano ali kukampu ya Bullets. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Timuyi ikufunanso itenge mnyamata wosewera pakati kutimu ya Azam, Yamikani Chester, koma timu yakeyi ikukaniza kuti wosewerayu sali pamalonda. +Bullets yatenganso Chisomo Mpachika wosewera kumbuyo mtimu ya Dedza Young Soccer ngakhale timu yake ikukaniza kumugulitsa ponena kuti ngati Bullets ikumufuna ndiye iwapatse Sankhani Mkandawire ndi Yamikani Fodya. +Tipite ku Silver Strikers yomwe yakanika kutenga goloboyi wa Mighty Be Forward Wanderers Richard Chipuwa ndipo mmalo mwake yatenga Bester Phiri, yemwenso amagwirira pagolo ku Wanderers. +Padakalipano Wanderers yatchaja Silver kuti ipereke K2 miliyoni pokana kuti Silver itenge wosewerayu pangongole. +Silver yatenga kale John Banda yemwe adali pangongole ku Young Soccer kuchokera ku Evirom pamtengo wa K500 000. Timuyi ikufunanso kutenga mnyamata wosewera kumanzere chakumbuyo kwa Epac, Dalitso Mwase, pamtengo wa K2 miliyoni. +Nayo Wanderers ikufuna kutenga Boston Kabango kuchokera ku Epac pamtengo wa K3 miliyoni. Koma Silver ndi Fisd Wizards nawonso maso awo ali pa mnyamata yemweyu. +Wanderers ndi Bullets akulimbirananso Chester, yemwe Azam ikukanitsitsa kugulitsa. Wanderers yaonetsanso chidwi kufuna kutenga Kelvin Hara, Dave Mwalughali, George Hawadi ndi Hastings Banda komanso George Kasambara kuchokera kutimu ya Chilumba Barracks ngakhale timuyi ikukana kuti sakuwagulitsa osewera awo. +Timuyi ikufunanso itenge John Lanjesi wa Civo pamtengo wa K4.5 miliyoni. +Azam Tigers yatenga kale Abraham Kamwendo kuchokera ku Blantyre United ndipo yatoleranso osewera ena achisodzera pamene Moyale yatenga Komani Msiska yemwe akutsogola ndi zigoli ku Chilumba. +Red Lions yagula wosewera wapakati wa Zomba United Stanley Dube. +Mphunzitsi wa timuyi Collins Nkuna akuti wakhala akuyendayenda mmidzimu ndipo wapeza osewera ambiri mboma la Salima. +Civo United sikumveka kuti ikusaka osewera mitunda iti koma timuyi yaitanitsa Josophat Kwalira kuchokera ku Dedza Young Soccer. +Wizards yatola Godfrey Masonda. Fisd ikufunanso kugula Precious Msosa kuchokera ku Wanderers. +Msikawu utsekedwa pa 18 September usiku ligiyi isanayambirenso pa 19 September. +Gogo apezeka atafa atadulidwa manja, mwendo Gogo wina wa zaka 75 wapezeka atafa mnkhuti yokumbamo dothi loumbira njerwa mmudzi mwa Tebulo Gondwe ku Enukweni mboma la Mzimba, koma alibe manja ndi mwendo umodzi. +Malinga ndi mdzukulu wa gogoyu, Petrona Nkunika, Gogo Watson Mapala adachoka kunyumba kwake Lamulungu sabata ziwiri zapitazo atatsanzika mdzukulu wakeyo kuti akukaona achimwene ake pamtunda wa makilomita anayi. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Nkunika adati anthu a mmudzi wa Tebulo Gondwe adali odabwa pa 15 August polandira uthenga woti akaone munthu yemwe adapezeka atafa mderalo. +Kuchokera kumayambiriro a mwezi uno agogo tinali nawo pasiwa popeza mayi anga adamwalira. Tidakhala nawo mpaka tsiku losesa sabata ziwiri zapitazo pomwe adanditsanzika kuti akupita kwa achimwene awo, Nkunika adatero. +Iye adati sadafufuzenso ngati gogoyu adafika kwa mbale wawoyo. +Nkunika adati akuganizira kuti gogoyu adaphedwa chifukwa cha mkangano kaamba ka malo. +Iye adati pali magulu awiri omwe akukanganirana malo omwe ali pakati pa Enukweni ndi Kavala ndipo Mapala ndi amene amadziwa bwino mbiri yake. +Iye adati mmodzi mwa anthu omwe akukanganirana malowo adaospeza gogoyu kuti amupha sabata ziwiri zapitazo. +Ife tikuganizira kuti agogo adaphedwa ndi munthu yemwe adawaospezayu, Nkunika adatero. +Iye adati apolisi atafika pamalopo adapempha anthuwo kuti ayangane ziwalo zosowazo mtchire lozungulira deralo, koma sadazipeze. +Mneneri wa polisi mchigawo cha kumpoto, Morris Chapola, adatsimikiza za nkhaniyi koma adati adakali mkati mofufuza. +Anatchezera Wamboni, ine Msilamu Zikomo Anatchereza, Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ndinagwa mchikondi ndi mtsikana wa Mboni za Yehova mpaka ndinamuchimwitsa moti ndikunena pano kuli mwana wamphongo. Makolo ake atamufunsa ananditchula ineyo ndipo atandiitana ndi akwathu ndidavomera mlanduwo. Makolo a mtsikanayu adati ngati ndikufuna kuti zithe bwino ndilowe mpingo wawo kuti asakandisumire kukhoti komanso kuti ndizisamalira mwana wangayo. Ine sindikufuna kulowa mpingowo, koma mtsikanayu akuti akhoza kulola kulowa Chisilamu ngati makolo ake angalole. Kodi apapa ndiye nditani kuti mwanayu ndizimusamalira popanda kulowa mumpingo wawowo? Kodi nditani kuti mkaziyu ndimukwatire? BJ, Lilongwe BJ, Mwazingwadi, achimwene a BJ. Vuto lili apa ndi loti inuyo simufuna kulolera zofuna za makolo a mkazi munamuchimwitsayo koma mukufuna zanu ziyende basi! Sizikhala choncho mukafuna kulowa moyo wa banja. Kulolerana ndiye gwero la banja. Mkazi munamuchimwitsayo waonetsa kale chikondi chake kwa inu chifukwa akulolera kuti atha kukutsatirani ku Chisilamu bola makolo ake amulole, koma inu chikondi chanu nchoperewerako pangono chifukwa mukumenyetsa nkhwanga pamwala kuti simungayerekeze kulowa mpingo wa mkazi wanuyo. Mulungu ndi mmodzi, baba, mipingo ndiye njambirimbiri! Langizo langa apa ndi loti zonse zimatha nkukambirana. Ngati akuchikazi nawonso sakulolera zoti mwana wawoyo alowe Chisilamu, monga inuyo mmene mwakanira kuti simungalowe mpingo wa Mboni za Yehova, kwatsala njira imodzimuthabe kulowa mbanja, koma aliyense akhale ndi ufulu wokapemphera koma akufuna. Zikakaniza apo, ndiy kaya. Ndakhala ndikunena nthawi zambiri kuti banja si masewera; pamakhala zambiri zofuna kutsatidwa musanalowane, koma mukadya mfulumiza, mavuto ake amakhala ngati amenewa. Koma, baba, nzoona mungalephere kuthandiza mwana wanu kaamba ka kusiyana mipingo? Mwana adalakwa chiyani? Nzoona makolo a mkazi akukuletsani kuthandiza mwana wanu kaamba koti simunalowe mpingo wawo? Chonde, mwana yekhayo asavutike chifukwa cha nkhani yanu. Muzimuthandiza mjira iliyonse, makolo a mkazi ndikhulupirira sadzaona cholakwika mwana wanu akamalandira thandizo kuchokera kwa bambo ake omubereka. +Amandikakamiza zogonana Agogo, Ndine mtsikana wa za 17 ndipo ndili ndi chibwenzi chomwe chimandikakamiza kuti tiyambe kugonana. Nditani? Mwana wanga, musiye ameneyo, sadzakuthandiza! Ndipo wachita bwino kundiuza msanga za nkhawa yako. Anzako ambiri amakopeka ndi zautsiru ngati zimene akukukakamiza bwenzi lakolo ndipo mapeto ake ndi kutengapo mimba kapena matenda opatsirana pogonana. Anyamata kapena abambo ambiri si okonzeka kuvomereza kuti ndiwo akupatsa pathupi kapena matenda ndiye chimakutsalira, tsogolo lako nkupiratu pamenepo. Fatsa, mwana wanga, sunga khosi ndipo mkanda woyera udzavala! Ukadzisunga udzaona kukoma moyo wako onse utapeza mwamuna weniweni amene adzakukonde ndi mtima wake wonse, osati kamberembere amene akuti muzigonana panopa muli pachibwenzi. Umuuziretu kuti iwe si chidole choseweretsa. Asaa! Ofuna mabanja Ndikufuna mkazi wa zaka 19-23 komanso woopa Mulungu0881 131 533 Ndine mkazi wa zaka 33 ndipo ndili ndi mwana mmodzi. Ndili ndi kachilombo ka HIV koma ndikumwa mankhwala. +Ndikufuna mwamuna wa zaka 35-37. Wondifuna aimbe pa 0882 617 531 Ndine mwamuna wa zaka 35 ndipo ndi ana awiri. +Ndikufuna wachikondi woti ndikwatire, akhale Mkhristu wa zaka 25-30 wokhala ku Lilongwe konkuno. Akhale wokonzeka kukayezetsa magazi. Wondifuna andiimbire pa 0882 511 934. +Maphunziro alowa nthenya Okhudzidwa ndi ngozi akuphuphabe Nthawi ili cha mma hafu pasiti leveni (11:30 am) ndipo kunja kukutentha koopsa. Ena mwa ophunzira pasukulu ya pulaimale ya Chikoja kwa mfumu Osiyana Mboma la Nsanje akuphunzirira pansi pamtengo wopanda masamba, ena ali mmatenti momwe mukutentha molapitsa. Ofesi ya aphunzitsi ili pansi pamtengonso umene masamba ake adayoyoka. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Posakhalitsa wophunzira wa Sitandade 4 wakomoka chifukwa chotentha ndipo ophunzira anzake akudzithira madzi kumutu pofuna kuziziritsa matupi awo. +Awa ndiwo mavuto amene amanga nthenje pasukulu ya Chikojayi, yomwe idakhudzidwa ndi madzi osefukira. +Nazonso sukulu za Chingoli mboma la Mulanje ndi Mvunguti mboma la Phalombe akukumana ndi zokhoma zokhazokhazi. +Pamene patha miyezi 8 chichitikireni ngoziyi, nyumba za aphunzitsi, zimbudzi komanso mabuloko ndi maofesi a aphunzitsi sizidakonzedwe, zomwe zikupereka mantha kuti mavutowa angakhodzokere mvula ikayamba mwezi ukubwerawu malinga ndi azanyengo. +Wachiwiri kwa mphunzitsi wamkulu pasukulu ya Chikoja, Clement Seda, akuti ngati mvula itayambe ndiye zivutitsitsa. Panopa tikupirira dzuwa, koma ngati mvula ikayamba ndiye palibe chabwino, sukulu idzatsekedwa kaye. +Mboma la Nsanje, madzi osefukira adagwetsa sukulu ya Chinama ndi Namiyala. Izi zidachititsa kuti boma limange matenti kuphiri la kwa Osiyana kwa T/A Mlolo kuti ophunzira azikaphunzirirako pamene matenti ena adamangidwa kwa Chambuluka. +Kumangidwa kwa matentiwa, chidali chimwemwe kwa aliyense kuti basi athana ndi mavuto osefukira kwa madzi, koma lero kwaipa pamene mavuto ena afika mkhosi. +Seda akuti boma lidalonjeza kuti ayamba kuwamangira sukulu nthawi ya mvula isadayambe. Koma mpaka lero kuli chuu. +Adatimangira matenti asanu ndipo makalasi ena akuphunzirira panja. Poyamba tinkadandaula ndi ana amene ankaphunzira panja, koma pano tikudandaulanso ndi matentiwa chifukwa mukutentha kwambiri. Mwaona nokha kuti mwana wina kuti Sali bwino, mavuto amenewa achulukira chifukwa matenda amutu si nkhani, adatero Seda. +Seda adati aphunzitsi onse akukhala ku Fatima ndi Makhanga, womwe ndi mtunda wa makilomita osachepera 14. +Tikafulumira kufika kuntchito ndiye kuti ndi 8:30 mmawa kusonyeza kuti piriyodi imodzi imadutsa tisanafike, komanso chifukwa chotentha, ophunzira amaweruka mofulumira dzuwa lisadafike powawitsa. +Izi zikuchititsa kuti ana asaphunzire mokwanira, komanso ambiri sakubwera chifukwa cha mavuto amene tikukumana nawowa, adatero Seda. +Iye adati izi zachititsa kuti zotsatira za mayeso a Sitandede 8 chaka chino zikhale zosokonekera. Mwa ana 40 amene adalemba mayeso a PSLC, ana 4 okha ndiwo adakhoza pomwe chaka chatha ana ana onse 35 adakhoza. +Mu 2013 adalemba ana 85 ndipo onse adakhoza, mu 2012 ana 29 adalemba mayeso ndipo 27 ndiwo adakhodza. Sukuluyi yakhala ikuchita bwino kuyambira mmbuyo monse, adatero Seda, amene sukulu yake ili ndi ophunzira 900. +Koma mneneri muunduna wa zamaphunziro Manfred Ndovi adati timupatse nthawi kuti afotokozepo zomwe boma likuchita kuti lipulumutse ophunzirawa. +Nayo sukulu ya Chingoli pulaimale mboma la Mulanje akuti mavuto ndi ankhaninkhani malinga ndi DC wa mbomalo Fred Movete. +Chimangireni matenti palibe chimene chachitikapo, mabuloko sadayambe kumangidwa moti zivuta kwambiri mvula ikayamba koma ndangomva kuti mapulani alipo kuti mabuloko amangidwa, adatero Movete. +DC wa boma la Phalombe Paul Kalilombe akuti mbomalo mavutowa ndi ochepa kuyerekeza ndi maboma ena. +Sukulu ya Mvunguti ndiyo idakhudzidwa, makalasi awiri okha ndiwo akuphunzira mmatenti koma ena ali mmabuloko, adatero Kalilombe. +Maboma 15 ndiwo adakhudzidwa ndi ngozi ya madzi mu January chaka chino koma boma la Mulanje, Nsanje ndi Phalombe ndi omwe sukulu zidakhudzidwa. +Kudali kumapemphero a achinyamata Munthu aliyense ngakhale atakhala wachisodzera imakwana nthawi yomwe amayenera kusiya kusereula ndi kuchita zinthu zogwira mtima. +Sam Sambo, ngakhale adali wachisodzera, adakhala adalimba mtima pamene adakumana ndi Emelia Chaula pofuna kumuuza za kumtima kwake. +Watengeratu basi: Sam ndi Emelia patsiku la ukwati wawo Emelia ndi mphunzitsi wa kupulaimale pomwe Sam akugwira ntchito ndi bungwe la God Cares Orphan komanso amachita zisudzo ndipo ndi wapampando wa bungwe la Theatre Association Northern Chapter. +Sam atamuona Emelia sadaugwire mtima koma tsiku lomwelo adamuuza za kugunda kwa mtima wake podziwa kuti bobobo samuthandiza ndipo akachedwetsa ena angamulande njoleyo. +Sam adati iye adamuthira diso koyamba Emelia kumapemphero a achinyamata ndipo naye msungwana sadachedwe kugonekera khosi Sam atamuuza mawu achikondi. +Mnyamatayu adalonjeza kuti iye wake ndi Emelia ndipo akazi ena adalibe nawonso ntchito ndipo kuchokera pomwepo Sam sadayanganenso akazi ena kufikira tsiku la ukwati wawo. +Awiriwa adamanga woyera kumpingo wa St Andrews CCAP ku Mzuzu ndipo madyerero adachitikira pa Victory Temple ku Mzuzu komweko pa 11 July chaka chino. +Sam adaululira Msangulutso kuti iye adagwa mchikondi ndi Emelia kaamba ka mtima wake wolimbikira ndi wodzipereka pantchito ya Mulungu. +Emelia amachokera mmudzi mwa Kawazamawe, Themba la Mathemba (Paramount Chief) Chikulamayembe mboma la Rumphi ndipo ndi woyamba kubadwa mbanja la ana asanu. Sam ndi wa mmudzi mwa Yobe Sambo Inkosi Mtwalo mboma la Mzimba ndipo ndi wachiwiri kubadwa mbanja la ana asanunso. +Banja latsopanoli lati silikufuna banja losalimba ngati mabanja ambiri amasiku ano ndipo iwo anenetsa kuti nthawi zonse aonetsetsa kuti akuika Mulungu patsogolo. Iwo ati nthawi zonse akakhala ndi vuto amayangana kwa Mulungu osati kupita kwa anthu omwe akhoza kukulitsa kavuto kakangono. +Ntchito ilipo Zilikoliko mawa lino kubwalo la masewero la Kamuzu Stadium kumene mphunzitsi wa timu ya dziko lino Ernest Mtawali akuyembekezeka kutsogolera anyamata ake kuchita chamuna chogonjensa Tanzania ndi kudzigulira malo mumpikisano wa 2018 World Cup. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Kuti ipitirire mndime ina ya mpikisanowu, timu ya Malawi ikuyenera kuchinya zigoli zosachepera ziwiri pambali polepheretsa alendo a kumpoto kwa dziko linowa kukoleka mpira muukonde. +Mtawali akuti mawa Flames idya monona Izi zili chonchi potsatira kugonja kwa Flames 2-0 pabwalo la Benjamin Mkapa ku Tanzania Lachitatu. Malawi itapambana 3-1 mmasewero achiwiri mawa, idzafanana zigoli ndi alendowa koma siidzakhalabe ndi mwayi wodumphira mu ndime ina ya mpikisanowu chifukwa malamulo amati zikatere, yemwe adapeza chigoli pabwalo la ena ndiwo akatswiri. +Koma mpira ukathera 2-0 mokomera Amalawi, tikhala kuti tafanana mphamvu ndipo pakayenera kulowa mndime ya kapherachoka wa mapenote kuti papezeke oyalula mphasa ndi kulowa mndime yachiwiri yodzakumana ndi timu ya dziko la Algeria. +Nzotheka kupambana ndi zigoli zochuluka Lamulungu likudzali. Tinaluza ku Tanzania chifukwa chochinyitsa zigoli zopepera. Koma pano mavuto onse takonza ndipo tili okonzeka kuchotsa chitonzo chomwe tili nacho pakalipano, adatero Mtawali msabatayi. +Komadi timumvere mphunzitsiyu zoti chilipo chipambano chokwanira mawa? Sitigwiritsidwanso fuwa la moto? Zitengera ndi mmene alowetsere osewera komanso momwe osewerawo adzadziperekere. Nkofunika tidzalimbikire kuthira nkhondo kutsogolo kwathu mowirikiza. Komanso tisadzawapatse adani mpata wobwerabwera kugolo lathu. Mwayi ulipo, adatero kadaulo woona za masewero a mpira Charles Nyirenda. +Nyirenda, yemwe adakhalapo mkulu wa bungwe la masewero a mpira mdziko muno la FAM, adaonjezera kuti ochemerera mpira asadzafooke polimbikitsa osewera a dziko lino ndi mingoli yopereka chikhulupiliro. +Pamene Malawi imakomana ndi Tanzania Lachitatu, Mtawali adali atachotsa komanso kuonjezera osewera ena amene adapatsidwa mpata mmasewero okumana ndi Swaziland kwawo mumpikisano wa Africa Cup of Nations omwe adathera 2-2. +Iye adachotsa John Lanjesi kumbuyo ndi kuseweretsapo Miracle Gabeya ndipo adachotsanso Richard Chipuwa pagolo ndi kuikapo Simplex Nthala. Kutsogolo, adaikako Chawanangwa Kaonga mmalo mwa Chiukepo Msowoya yemwe adavulala. +Agundidwa akuthawitsa katundu wakuba Bambo wina wagundidwa ndi galimoto ku Mzuzu pomwe amathawitsa mapaketi awiri a khofi omwe amamuganizira kuti adaba pa Mzuzu Coffee Den. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Bamboyo, yemwe ndi Laston Kaunda wa zaka 32 ndi wochokera mmudzi mwa Chiphanzi, T/A Nkumbira mboma la Nkhata Bay. +Mneneri wapolisi mumzinda wa Mzuzu, Patrick Saulosi, adati mnyamatayo adapita ku Coffee Den mmawa wa Lachiwiri sabata yatha ndi nsuweni wake komwe adakanyamula mapaketi a khofiwo. +Woganiziridwayo akutuluka mu Coffee Den muja adatuluka ndi mapaketi awiri a khofi osalipira. Mnyamata wogwira ntchito pamalopo ataona zomwe amachita Kaunda adayamba kumuthangitsa, adafotokoza Saulosi. +Saulosi adati pa nthawi yomwe Kaunda amafuna kuoloka nsewu galimoto idamuomba ndipo iye adavulala kwambiri mwendo. +Iyeyo ali kuchipatala cha Mzuzu Central Hospital (MCH) koma akangotuluka kuchipatalako atengedwa ndi apolisi pamlandu wakuba, adatero Saulosi. +Saulosi adati kaamba ka kuchepa kwa mlanduwo palibe wapolisi amene akudikirira Kaunda kuchipatala podikirira mlandu. +Msangulutso utapita kuchipatalako udakumana ndi Kaunda yemwe akadali mchipatala kulandira thandizo. +Kaunda adati sakukumbukira chilichonse chomwe chidachitika patsikulo chifukwa adali ataledzera kwambiri. +Sindikudziwa chomwe chidachitika ndidangozindira kuti ndili kuchipatala kuno, iye adayankha motero. +Anjata wopezeka ndi mitengo ya tsanya Apolisi ku Lilongwe Lachitatu adanjata nzika ya ku China chifukwa chomuganizira kuti adapezeka ndi mitengo ya tsanya yomwe nzikayo imafuna kutumiza kwawo kuti ikasake misika. +Nzikayi adaigwira pabwalo la ndege la Kamuzu International Airport dzuwa lili paliwombo pamalo ochitira chipikisheni pabwalo la ndegelo ndipo akuti katunduyo amafuna kumukwenza ndege yopita kwawo kudzera ku Ethiopia. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Apolisi a pabwalo la ndegelo adati mkuluyo, Lin Jie, adavomera mlanduwo ndipo adati mitengo yomwe amafuna kutumiza kwawoko idali yokafufuzira msika chabe kuti msikawo ukapezeka, ayambe bizinesi yotumiza mitengoyi kwawo. +Yemwe amatanthauzira pakati pa apolisi ndi mkuluyo, Shi Qi Bine, adanena mosapsatira kuti iye amafuna kuyamba bizinesi yogulitsa mitengoyi kunja ndipo yomwe amatumizayo idali yokangoonetsa chabe, adatero Sapulani Chitonde, mneneri wa polisi pabwalo. +Iye adati Lin Jie adauza apolisiwo kuti dziko la Malawi likufunika anthu ngati iye amasomphenya ofuna kupeza njira zina zopezera ndalama osati kudalira njira zamgonagona. +Mkuluyu adabwera mdziko muno mwezi wa May chaka chino ndipo amakhala mumzinda wa Lilongwe. +Malingana ndi malamulo a dziko lino, ndi mlandu kupezeka ndi zamnkhalango popanda chilolezo chilichonse ndipo apolisi ati adzathana ndi aliyense wopezeka ndi katundu wamnkhalango mwachinyengo kapena wofuna kutulutsa katundu woletsedwa kudzera pabwalo la ndegeli. +Kumapeto a mwezi watha, apolisi adagwira nzika inanso ya ku China aipeza ikufuna kuzembetsa minyanga ya njovu yoduladula mapisi nkuibisa mchikwama ndi cholinga choti apite nayo kwawo. +Amati aukitsa wakufa koma athera mzingwe Mudali fumbi mmudzi mwa Mpheziwa kwa T/A Kasumbu mboma la Dedza posachedwapa pamene khwimbi la anthu lidakhamukira mmudzimo kukaonerera ntchito ya asinganga atatu omwe amati atha kuukitsa wina kwa akufa. +Mapeto ake awiri mwa atatuwa adathera mmanja mwa apolisi ndipo pano akuyankha mlandu wopanga upo wofuna kuchita chinyengo pamene wachitatuyo adati phazi thandize ndipo mpaka pano apolisi akumusakasakabe. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Gulupu Chinyamula, mkazi wa malemuyo ndi mneneri wa polisi ya Dedza, Edward Kabango, atsimikiza za nkhaniyi. +Malinga ndi Kabango, oganiziridwawo ndi Gift Phiri, Jemitala Alfred, komanso wina amene akungodziwika ndi dzina loti Masambaasiyana. +Atatuwa akuti amadzithemba kuti ali nayo mphamvu youkitsa munthu kwa akufa ndipo adati ngati anthu ali ndi chikaiko aonera pa Evance Bunya, yemwe adamwalira pa 15 May chaka chino atadwala mutu kwa sabata imodzi. +Mkazi wa malemuyo, Rose Bunya, adauza Msangulutso Lachinayi lapitali kuti asingangawo adabwera ndi mnzake wa mayiyu yemwe amati amathandiza kuukitsa munthu kwa akufa. +Gunya adati, Iwo atabwera adandiuza kuti malemu amunanga adachita kusowetsedwa mmatsenga kotero ngati ndingafune atha kupanga mankhwala ndipo angathe kubwera nkukhalanso moyo. +Koma ngakhale asingangawa amati malemuyo adachita kusowetsedwa mmatsenga, Gunya adati mwambo wonse wa maliro udayenda bwinobwino ndipo mwamuna wake adakaikidwa kumanda monga achitira ndi maliro onse. +Gulupu Chinyamula, yemwe amayanganiranso mudzi wa Mpheziwa, adati asingangawo adatchaja ndalama pafupifupi K400 000 ngati akufuna kuti malemuyo abwere komwe amati adamupititsako mmatsenga. +Mmudzimo anthu adali kalikiriki kusonkherana, apa nkuti ine kulibe, ndipo adapeza ndalama zoposera K200 000 zomwe akuti adachita kukongola kwa anthu pamene zina zidaperekedwa ndi achibale a malemuwo, adatero Gulupu Chinyamula. +Akuti asingangawo adakana kulandira ndalamayo ponena kuti yachepa ndipo mayi Bunya adaperekanso wailesi. Apa mpomwe akuti asingangawo adawatsimikizira kuti malemuyo atulukira. +Malinga ndi Kabango, pa 31 July wapitayu ndilo tsiku lomwe oganiziridwawa amati achite matsengawo kuti wakufayo atulukire pamaso pa abale ake dzuwa likuswa mtengo. +Anthu adasonkhana ndipo kudali zoimba, komanso kudakonzedwa zakudya kuti anthu adye uku akudikira kuti malemuyo atulukire. Mosakhalitsa, kudatulukira asinganga awiri ndipo adafunditsa nsalu munthu mmodzi amene amati ndi wouka kwa akufayo. +Adamulowetsa mnyumba ya malemuyo ndipo adati ngati munthu akufuna kukamuona bamboyo alipire K1 000, adatero Kabango. +Koma mwambowu akuti udasokonekera pamene Gulupu Chinyamula adamva za nkhaniyi. +Ngakhale amanamiza anthu kuti angathe kuukitsa munthu kwa akufa, ine sindidakhulupirire ndiponso amalephera kufotokoza bwino kuti anthu akhulupirire. Ndiye ndidangowathira zingwe ndi kuitana apolisi kuti adzawatenge, adatero Chinyamula. +Kabango watsimikizira zakunjatidwa kwa Phiri ndi Alfred ndipo wati apolisi akusakasakabe Masambaasiyana yemwe akumuganizira kuti ndiye amatsogolera zochitikazo. +Masambaasiyana akuganiziridwanso kuti ndiye adalandira ndalamazo, ndiye kafukufuku ali mkati, adatero Kabango. +Kabango adati omangidwawa atsekuliridwa mlandu wopanga upo wofuna kuchita chinyengo. +Iwo akuti adaonekera kubwalo la milandu Lachitatu pa 12 August koma akhoti awapatsa belo. +Apolisi alandira uphungu paziphuphu Bungwe lolimbana ndi mchitidwe wa ziphuphu ndi katangale la Anti-Corruption Bureau (ACB) laphunzitsa apolisi a mumzinda wa Mzuzu za momwe angapewere mchitidwewu. +Malingana ndi kafukufuku yemwe lidachita bungwe la Centre for Social Research mu 2013 nthambi ya polisi ya Road Traffic and Safety Services lidapezeka kuti ndiyo ili patsogolo polandira ziphuphu komanso kuchita za katangale mdziko muno. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Kafukufukuyo adapezanso kuti nthambi ya Road Traffic Commission nayo ili patsogolo kuchita mchitidwewu. +Mmodzi mwa akuluakulu olimbana ndi mchitidwewu kubungwe la ACB, Patrick Mogha, adati iwo adachiona chofunika kuti awaphunzitse apolisi komanso anthu a madera ozungulira pankhani za ziphuphu kuti athandize kuchepetsa mchitidwewu. +Tidaona kuti ndi chinthu chanzeru kuti tiwaphunzitse a polisi za momwe angapewere kapena kudziteteza kumchitidwe wakatangale ndi ziphuphu. Tidazindikira kuti anthu ena pochita mchitidwewu sadziwa kuti akulakwira malamulo komanso akubwezeretsa chitukuko cha dziko mmbuyo, adatero Mogha. +Mogha adaonjeza kuti iwo ali ndi chikhulupiriro kuti akaphunzitsa apolisi zithandiza kuchepetsa mchitidwewu. +Wachiwiri kwa komishonala wa polisi, yemwenso ndi mkulu wa nthambi yoonetsetsa kuti apolisi akuchita zinthu moyenera (Professional Standards Unit), Esther Wandale, adati iwo ali ndi cholinga chothana ndi mchitidwe wa katangale ndi ziphuphu pakati pa apolisi ndipo ati ali ndi chikhulupiliro kuti zinthu zisintha. +Cholinga chathu ndi kulimbikitsa apolisi athu kuti azikhala otsata malamulo komanso odalirika. Izi ndi zikhoza kutheka pokhapokha iwo akudziwa kuti katangale ndi chiyani kwenikweni, adatero Wandale. +Mmodzi mwa oyendetsa galimoto zahayala (taxi), Happy Soko, adati akuona kuti maphunzirowa athandiza kuchepetsa mchitidwe wa ziphuphu ndi katangale pamsewu. +Iye idadati apolisi ndi omwe amathandiza kulimbikitsa mchitidwewu pamsewu chifukwa akadakhala kuti amatsatira malamulo moyenera si bwezi oyendetsa galimowo akuchita mchitidwewu. +Maphunzirowa athandiza koma ndikuona kuti akadaphatikizanso anthu ngati ife zikadathandiza kuthana ndi vutoli mwachangu, adatero Soko. +Asaka ofukula manda ndi kutengamo ziwalo Apolisi ku Kanengo mumzinda wa Lilongwe ati akufunafuna anthu aupandu omwe adafukula manda ndi kudula ziwalo za mtembo wa mtsikana yemwe adamwalira masiku angapo apitawo mmudzi mwa Mgona, mdera la T/A Chitukula mboma la Lilongwe. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Akuti awa ndi malodza: Wisiki Pofotokoza nkhaniyi, mneneri wa polisi ya Kanengo, Esther Mkwanda, adati iwo adalandira lamya yonena kuti anthu ena achipongwe, omwe zolinga zawo sizikudziwika bwino, adafukula manda ndi kudula ziwalo zingapo za mtembo wa Maria Roja, wa zaka 18, yemwe adamuika mmandamo. +Chimene chidachitika nchakuti ifeyo tidangolandira foni mmamawa yonena kuti anthu apeza manda ofukulidwa kwa Mgona. Ife tidathamangirako ndipo tidapeza kuti mandawo ndi ofukulidwadi ndipo kuti thupi lili mdzenje momwemo koma atalichotsa mbokosi lomwe adachita chophwanya, adafotokoza Mkwanda pouza Msangulutso. +Adapitiriza kunena kuti adapeza kuti achipongwewo adachotsa maso, lilime, milomo, chala chamkombaphala chakumanzere, komanso ziwalo zobisika. +Iye adati adachita kukhomanso bokosilo mothandizana ndi anthu a mmudzimo ndipo adaikanso thupilo mmandamo. +Mkwanda adati ngakhale apolisi sadagwirebe wina aliyense pankhaniyi, iwo ayesetsa kuti omwe adachita khalidwe lachilendoli agwidwe kuti akayankhe mlandu kukhothi. +Mayi Janet Wisiki, yemwe ndi mayi ake aangono a malemuyo, adati zomwe zidachitikazo ndi malodza enieni. +Ine ndikuluphera kugona poganizira kuti kodi chandiona ine ndi chiyani? Kapena nditi chikunditsata ine ndi chiyani pamalodza oterewa? Kunena zoona, anthu amenewa andilaula ine. Ngakhale makolo anga zoterezi sadazionepo, adatero Wisiki, akusisima. +Mayiyu, yemwe ali ndi zaka 40, kwawo kwenikweni ndi mmudzi mwa Jeriko, mdera la T/A Pemba, mboma la Dedza. Akuti adabwera ndi kukhazikika kwa Mgonako zaka 30 zapitazo. Iye ati chomvetsa chisoni chinanso nchakuti Maria, yemwe adali mwana wa mchemwali wake wamkulu, wamwalira ali wachisodzera. +Malinga ndi Wisiki, Maria adamwalira atadwala malungo. +Miyoyo ya Amalawi ili pachiopsezo Mkulu wa bungwe loona za umoyo la Malawi Health Equity Network (MHEN) Martha Kwataine wati nzomvetsa chisoni kuti dziko la Malawi lasemphanitsa zoyenera kuika patsogolo. Iye wati izi zaika miyoyo ya Amalawi ambiri pachiospezo. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Kwataine adanena izi kaamba ka ganizo la boma losiya kulemba ntchito madokotala 51 omwe amaliza maphunziro awo kusukulu ya ukachenjede ya College of Medicine ati popeza bomalo silikulembanso anthu ntchito. +Koma unduna wa zaumoyo wati wasintha maganizo ake ndipo tsopano ulemba ntchito madokotalawa ngakhale kumene kuchokere ndalama zowalipira sikukudziwika. +Polankhulana ndi Tamvani mkati mwa sabatayi, Kwataine adati nzachisoni kuti boma lafika pokanika kulemba ntchito adotolo panthawi yomwe dziko lino likulira chifukwa chakuchepa kwa madotolo mzipatala. +Iye adati nzodabwitsa kuti boma lomwe lakhala likudandaula kuti madokotala akuthawa mdziko muno kutsatira ntchino zonona kunja, pano likukana kuwalemba ntchito. +Nanga akatithawa, kapena anthu akasiya kupita kusukulu ya udotolo, titani? adadabwa Kwataine. +Iye adati nzachisoni kuti ganizo la boma posalemba ntchito madotokotalawa kuika miyoyo ya Amalawi ambiri pachiospezo chifukwa madokotala alipo kale ochepa. +Ndikulankhula pano zinthu sizili bwino mzipatala zambiri momwe anthu akumwalira ndi matenda ochizika kaamba kakuchepa kwa madotolo, Kwataine adatero. +Ndipo msabatayi madokotala onse mdziko muno adaopseza kuti anyanyala ntchito ngati boma sililemba ntchito anzawowo pakutha pa sabata ziwiri. +Koma pozindikira kuti zinthu sizikhala bwino madokotalawo akanyanyala ntchito, unduna wa zaumoyo ndi a kuunduna wa zachuma adakhala pansi nkugwirizana kuti madokotalawo alembedwe ntchito zisanafike poipa. +Mneneri wa unduna wa zaumoyo Adrian Chikumbe adatsimikiza za nkhaniyi Lachinayi polankhula ndi mtolankhani wa The Nation, koma adati undunawo sukudziwa kuti ndalama zolipira madokotala atsopanowo zichokera kuti. +Naye mneneri wa unduna wa zachuma Nations Msowoya adati ngakhale adagwirizana zoti madokotalawo ndi anamwino alembedwe ntchito, sakudziwa kuti malipiro awo azitenga kuti. +Malinga ndi kalata yomwe adatulutsa a bungwe la Medical Doctors Union of Malawi mogwirizana ndi bungwe la Society of Medical Doctors, kulemba ntchito adotolowa kuthandiza kuchepetsa kuperewera kwawo mzipatala. +Kalatayo idati boma la Malawi liganizire za umoyo wa anthu mdziko muno womwe ukufunika kuikidwa patsogolo ndipo zina zonse zibwere pambuyo.n Mkulu wa bungwe loona za umoyo la Malawi Health Equity Network (MHEN) Martha Kwataine wati nzomvetsa chisoni kuti dziko la Malawi lasemphanitsa zoyenera kuika patsogolo. Iye wati izi zaika miyoyo ya Amalawi ambiri pachiospezo. +Kwataine adanena izi kaamba ka ganizo la boma losiya kulemba ntchito madokotala 51 omwe amaliza maphunziro awo kusukulu ya ukachenjede ya College of Medicine ati popeza bomalo silikulembanso anthu ntchito. +Koma unduna wa zaumoyo wati wasintha maganizo ake ndipo tsopano ulemba ntchito madokotalawa ngakhale kumene kuchokere ndalama zowalipira sikukudziwika. +Polankhulana ndi Tamvani mkati mwa sabatayi, Kwataine adati nzachisoni kuti boma lafika pokanika kulemba ntchito adotolo panthawi yomwe dziko lino likulira chifukwa chakuchepa kwa madotolo mzipatala. +Iye adati nzodabwitsa kuti boma lomwe lakhala likudandaula kuti madokotala akuthawa mdziko muno kutsatira ntchino zonona kunja, pano likukana kuwalemba ntchito. +Nanga akatithawa, kapena anthu akasiya kupita kusukulu ya udotolo, titani? adadabwa Kwataine. +Iye adati nzachisoni kuti ganizo la boma posalemba ntchito madotokotalawa kuika miyoyo ya Amalawi ambiri pachiospezo chifukwa madokotala alipo kale ochepa. +Ndikulankhula pano zinthu sizili bwino mzipatala zambiri momwe anthu akumwalira ndi matenda ochizika kaamba kakuchepa kwa madotolo, Kwataine adatero. +Ndipo msabatayi madokotala onse mdziko muno adaopseza kuti anyanyala ntchito ngati boma sililemba ntchito anzawowo pakutha pa sabata ziwiri. +Koma pozindikira kuti zinthu sizikhala bwino madokotalawo akanyanyala ntchito, unduna wa zaumoyo ndi a kuunduna wa zachuma adakhala pansi nkugwirizana kuti madokotalawo alembedwe ntchito zisanafike poipa. +Mneneri wa unduna wa zaumoyo Adrian Chikumbe adatsimikiza za nkhaniyi Lachinayi polankhula ndi mtolankhani wa The Nation, koma adati undunawo sukudziwa kuti ndalama zolipira madokotala atsopanowo zichokera kuti. +Naye mneneri wa unduna wa zachuma Nations Msowoya adati ngakhale adagwirizana zoti madokotalawo ndi anamwino alembedwe ntchito, sakudziwa kuti malipiro awo azitenga kuti. +Malinga ndi kalata yomwe adatulutsa a bungwe la Medical Doctors Union of Malawi mogwirizana ndi bungwe la Society of Medical Doctors, kulemba ntchito adotolowa kuthandiza kuchepetsa kuperewera kwawo mzipatala. +Limbani Simenti: Kukangalika pa zoimba Ku Malawi kuno kuli oimba zauzimu ochuluka. Mmodzi mwa iwo ndi Limbani Simenti yemwe akudziwika bwino. Iyetu amadziwika kwambiri ndi nyimbo ya Ndikuoneni. CHIMWEMWE SEFASI adamupeza mnyamata wa ku Ndirandeyu ndipo adacheza naye motere: Ndikudziwe. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Dzina langa ndine Limbani Simenti, ndimachokera chigawo cha kumwera, mboma la Thyolo, T/A Nsabwe, mmudzi wa Matekenya. +Adaimba Ndikuoneni Baba: Simenti Kodi zoimbaimbazi mudayamba liti? Inetu zoimbaimba ndidayamba pa kanthawi, pamene ndidali sitandade 4, koma chidwi chidayamba kundipeza pomwe ndidayamba kuimba kwaya ya Mount Sinai mu 1999. Mu 2010 pomwe ndidayamba kuimba mu Praise Team ya mpingo wa All for Jesus. Mu 2011 mpomwe ndidatulutsa chimbale changa cha Lungisani Mpiro kutanthauza kuti konzani moyo wanga. +Kodi nkhani zamaimbidwe umaziona bwanji pa Malawi pano? Nkhani za maimbidwe zili bwino pa Malawi. Kungoti ubwino weniweni umaoneka munthu ukakhala ndi chidwi komanso ukaikapo mtima wako wonse, ndi kudziwa chomwe ukufuna pamoyo wako chifukwa zomwe umabzala ndi zomwe umakolola. +Kodi nyimbo yako ya Ndikuoneni imatiphunzitsanji? Ndikuoneni Baba ndi nyimbo yomwe mumapezeka mphamvu. Iyi ndi nyimbo yomwe imatifupikiritsa chifupi ndi Mulungu. Mwachitsanzo, ndikamati Baba ndifuna ndikuoneni imakhala ikusonyeza ife tili paubale weniweni ndi Mulungu, ndi nyimbo yomwe ine uthenga ndimati ndikaumva ndimaona kuti Mlengi ndi amene adandipatsa uthengawo kuti ndilakhule kudzera mnyimbo posonyeza kuti nkhawa zathu timatula kwa Yehova ndi kuonetsa ubale weniweni ndi Mulungu. Nyimbo imeneyi imapezeka mchimbale chotchedwa Lungisani Mpiro chomwe mudali nyimbo 12 monga Uligwindi, Njoka Yokalamba, Yesu Salemphera ndi zina, pamene DVD idatuluka ndi dzina loti Ndikuoneni. +Kodi chaka chino Amalawi ayembekezere zotani kuchoka kwa iwe? Ndikuwalonjeza Amalawi kuti tisanafike kumapeto a chaka chino cha 2015 ndiwapatsira chimbale chomwe chili ndi nyimbo 12, zomwe panopa ndamaliza kujambula. +Kwagwedezeka ku PP Potsata mawu a mtsogoleri wakale wa dziko lino Bakili Muluzi onena kuti chipani cha MCP chatha ngati makatani, zikuoneka kuti chipani cha Peoples Party (PP) nacho chikutsatira momwemo. +Izi zili choncho malinga ndi mgwedegwede womwe wabuka mchipanichi pamene ena akufuna kubweretsa Khumbo Kachali kuti akhale wogwirizira mpando wa pulezidenti wa PP mmmalo mwa Joyce Banda yemwe sali mdziko muno. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Chipwirikitichi chachititsa kuti ena amaudindo awo, monga mkhalakale kuchipanichi Stephen Mwenye, achoke mchipanichi. +Kuchoka kwa Mwenye kukutsatiranso kusonthoka kwa yemwe adali wachiwiri kwa pulezidenti wa chipanichi kuchigawo chakummwera Brown Mpinganjira ndi Harry Mkandawire wa chigawo chakumpoto. +Koma kulankhula kwa Banda kwakhala koti mndale za zipani zambiri, aliyense ali ndi ufulu wolowa chipani chilichonse chomwe akufuna ngakhale kuchokamo. +Pano kuchipaniku kwavuta potsatira zomwe mkulu wa chipanichi kumpoto Mbusa Christopher Mzomera Ngwira adachita polengeza poyera kuti Kachali ndiye mtsogoleri wogwirizira wa chipani cha PP mmalo mwa Banda, yemwe chilepherereni pachisankho cha pulezidenti wa dziko lino mu May chaka chatha adakali kunja. +Ganizoli silidavomerezedwe ndi akuluakulu ena mchipanichi monga wachiwiri kwa pulezidenti mchigawo chapakati, Uladi Mussa, yemwe wachenjeza Ngwira pa zochita zake. +Wina asalote zoika munthu wina pampando wa pulezidenti mosatsata njira yake, adatero Mussa. +Iye adati ndi kuphwanya demokalase kuti chigawo chimodzi chingovumbuluka ndi kusankha mtsogoleri wina zigawo zina osadziwa, koma nkumayembekeza kuti zigawo zomwe sizidasankhe nawozo zitsatire mtsogoleriyo. +Joyce Banda adakalibe mtsogoleri wathu. Sadatule pansi udindo wake. Tiitanitsa mkhumano wa akuluakulu a chipanichi kuti tisankhe mlowammalo wake, adatero Mussa. +Mwambo wopha mudzi poika mfumu Anthu ena amakhulupirira kuti akamwalira amayenera akaikidwe chatsonga kapena kuti chokhala. Izi zimachitika kwambiri pakati pa mafumu Achingoni maka a kwa Maseko. Umu ndi momwe zidakhalira ndi maliro a T/A Bvumbwe wa ku Thyolo mwezi wathawu, yemwe adaikidwa chatsonga. Anthu otere akamwalira, pamakhala mwambo wopha mudzi. Izi zimachitika pokumba nyumba yoti igone mfumuyo. BOBBY KABANGO akutsata momwe zimakhalira. +Pepani wawa ndi zovutazi. Koma ndimati tichezepo pangono za miyambo ina yokhudza maikidwe a mfumu Yachingoni. Koma poyamba tidziwane. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Ndine Opesi Mangombo ndipo kwathu ndi mommuno mwa Bvumbwe. +Ndinu wa mtundu wanji? Mukadzaona nsalu ya Gomani chonchi komanso mthini pamutu, musadzafunse, dziwani kuti amenewo ndi Angoni ankhondo aja amene adachoka ku Mozambique ku Domwe. Moti ine ndi Mngoni, ndili kumtundu wa Bvumbwe. +Ndamva kuti inu ndiye mumatsogolera adzukulu okumba manda a mfumu Mwamva zoona koma si kuti ndi manda onse, koma kuti ndinatsogolera adzukulu amene akumba manda amene tiike thupi la mfumu yathu Bvumbwe. +Timamva za mawu oti kupha mudzi pamene mukukumba manda ogona mfumu, zimatanthauzanji? Choyamba dziwani kaye kuti mfumu yathu igona chatsonga, kupha mudzi kumachitika ngati mukukumba manda a munthu amene akaikidwe chatsonga. Kwa iwo okaikidwa chogona ndiye sikukhalanso kupha mudzi. Mudzi ndi malo kapena kuti phanga lomwe mfumuyo imaikidwako. Choyamba mumakumba dzenje lotalika ndi mamita atatu ndi theka. Limakhala dzenje lozungulira, osati lamakona anayi monga zikhalira ndi ena. Mukamaliza kukumbako ndiye mumakhala pansi kupanga mudziwo. +Fotokozaninso, mwati mudzi nchiyani? Mudzi ndi malo kapena kuti phanga lomwe mfumu igoneko. Pamene mwakumba ndi kumaliza manda, ndiye mumayamba kupanga phanga. Kukula kwake kufanane ndi kukula kwa bokosilo. Koma nthawi zambiri mudziwo umakula ndi mamita awiri mlitali ndi mlifupi. +Ndiye mukati kupha mudzi mumatanthauza chiyani? Timatanthauza ntchito yomwe mumachita kuti muyambe kupanga phangalo lomwe kulowe mfumu yathu. +Zimatheka bwanji kuti mupange phanga loti muli kale mdzenje? Timaonetsetsa kuti dzenjelo likhale lokula bwino kuti mukathe kukhala pansi ndi kumagoba mudziwo. Timapangira khasu lomweli koma timaligulula ndi kulizika ngati nkhwangwa. +Mukamaliza mumatani? Tikafikira mlingo womwe tikufuna, timatenga timitengo ndi kukhoma pakhomo pa mudziwo chifukwa bokosi likalowa, timayenera titseke pakhomopa kuti dothi lisalowe. Simungapange mudzi musadayeze kukula kwa bokosi lomwe mfumu yathu igonemo. +Dothi lakenso liti? Pajatu dzenjeli timalikwirira pamene taika mfumu yathu, ndiye pakhomo pa mudzi timatsekapo kuti dothi lisamupeze. +Koma cholinga chopangira mudziwu nchiyani? Mfumu siyenera kuthiridwa dothi pamutu. Mudziwu umapangidwa dala kuti ipeze kobisala pamene tikuthira dothi. +Ndi manda ngati awa, chiliza chake chimakhala chotani? Chimamangidwa mozunguliranso (akuloza ziliza za mafumu ena pamandapo) osati chogona monga zina zimakhalira. Malo ano ndi a mafumu okhaokha komanso akazi awo. Mwana wa mfumu sagona pano pokhapokha ngati wavekedwa ufumu. +Kodi uku sikungovutika chabe? Mwatero ndi inuyo koma ife sitiona kuvutika koma kukwaniritsa chikhalidwe chathu ndi ulemu kwa mafumu athu monga Angoni. +Chitukuko cha foni Ndati ndikuuzeni abale anzanga, mbale wina amene anatchona ku Jubeki ndipo anasungidwa ku Lindela kwa nthawi wafika pa Wenela. Chanzeru chimene wandibweretsera ndi foni yochonga. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Tsonotu lero nkhani si ya mtchona wamkulu Adona Hilida. Inde apa sindikambatu za kutha mphamvu kwa Kwacha chifukwa ngakhale Moya Pete alibe yankho lenileni! Sindinganene wamasiye wamkulu Shati Choyamba amene adathawa mkazi wake lero akutizunza ndi uthenga wakuti ndi wa masiye! Ndipo tili pankhani wa mkuluyu, ndidaona nyumba ina yozinga bwino msewu wa Fatima, tsono ndikudabwa kuti akukakamira mtauni bwanji? Sindinganene za Mpando Wamkulu chifukwa pano msana uja udapola ndipo wasiya zopita ndi mtsamiro kukhoti kukayankha zosolola ndi zina ndi zina. Abale, ndinganene chiyani za Lazalo Chatsika wa Male Chauvinist Pigs yemwe tsopano naye wayamba kuonetsa mawanga a gogo uja adandipeza nditavula polima kwathu kwa Kanduku ku Mwanza? Ngati simunamve, mfunseni Thursday Jumbo! Koma inu! Lero nkhani si ya Polisi Palibe, gulu limene likutha ngati makatani a China. Makatani ndi onse, koma pajatu belo siyinama! Nanga taonani Adona Hilida kutuma uja Ibula kuti achotse uyu wa chitaganya kenako Adona Hilidawo nkudzanena kuti ayi mkulu wa chitaganyayo asachotsedwe. +Inde, sitikamba za Pitapo yemwe tsopano akusimba lokoma apoooo! Chifukwa sabata imeneyi ndakhala ndi kuunguza nawo pa Facebook ndati ndiyalule zina ndi zina zimene ndakhala ndikuona. Nkhani yaikulu ndi ya kuzimazima kwa magetsi! Abale inu, we are living in the dark ages ndipo bungwe loonetsetsa kuti mdima ukufikira aliyense pano pa Wenela likadakhala chakudya bwenzi ali manyumwa. Musandifunse kuti chipatso chimenechi nchiti chifukwa sindkuuzani. Kuzolowera zipwete eti? Tsono mmodzi mwa anthu amene anaponya nkhani yake pa buku la nkhope (kaya ndi nkhope ya buku, sindidziwa) adatambasula zomwe anakumana nazo chifukwa cha kuzima kwa magetsi. +Mkazi wanga anandipeza ndi kucheza ndi mkazi woyendayenda. Anapita kunyumba kumene adakhutulira mafuta mpoto, nkuika pa cooker. Mkaziyo adayatsa cooker nkukagwira ntchito zina. Ntafika sanafunse kalikonse koma adaphula mafuta aja nkundikapiza. Samadziwa kuti nthawi amaika mafutawo pamoto, magetsi anazima ndipo mafuta sanawire. Zikomo Eeeeeeeishkom! Abale anzanga, ndikhulupirira madotolo a chipatala cha odwala misala aziyangana kaye zimene odwala awo akhala akulemba pomwe amayenda pamsewu ngati abwinobwino. +Ndipo nditaunguza Gervazzio, wa pamalo aja timakonda pa Wenela, ndidapeza kuti ali mgulu lina lotchedwa Kupeza Mabanja ndi Zibwenzi Pa Wenela! Chodabwitsa nchakuti iyeyo ali pabanja! Kodi Facebook yaphweketsa chiwerewere chomwechi? Ndikumadabwanso kuti nkatsegula tsambali, akumandifunsa kuti What is on Your Mind! Akadziwa ndiye amafuna nditani? Nkhawa zanga si zotulira anthu osadziwa? Ndiye pali ena akuponya zithunzi zolaula pa Facebook. Akakhalakhala, umva akunena kuti wina wawalowera kutsamba lawo! Mukunamiza ndani? Ngakhale zandipeza mochedwa Abiti Patuma adandiuza kale kuti amene zithunzi zotere zikuoneka patsamba pawo ndiye kuti adatsegula zithunzi zotere patsamba la ena! Usawi, chichi? Kukamba za Abiti Patuma, sabata iyo adanditengera ku ukwati wina umene udali pamalo ena oyandikira pa Wenela. Kudali mwana wa munthu ku ukwati umenewo. +Itafika nthawi yofupa akuchimuna, ndinadabwa aliyense ali pa foni yake. Nanenso ndidalowa nawo mgulumo, nkumaseweretsa foni yanga. Nkatere, kutola zithunzi za anthu ali kakaka ndi mafoni awo, popanda wofupa. +Nkatero, ndaponya kale pa Facebook. Kungoponya kenako nkupanga like. Nthawi yomweyo nkudzaponya comment: Life is good#embarassed with lasanje! Akuchimunawo adapitiriza kuseweretsa mafoni awo, popanda wofupa olo mmodzi. +Titabwerera kukakhala pansi ndidafunsa Abiti Patuma kuti akuchimuna kuumira kwanji kotere? Kungopita mbwalo kukavina mmalo mofupa! Anthu a nkhanza, satana ali bwino, ndidatero. +Abiti Patuma adaseka ngati wakwatiwa kumene. +Kikikiki! Tade mudzatsala. Anthuwatu akufupa kupyolera pa Mpamba, Airtel Money komanso achina Mo626 ndi njira zina zosamutsira ndalama pafoni, adanditsegula mmaso Abiti Patuma. +ANATCHEZERA Akundikaikira Anatchereza, Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ndine mtsikana wa zaka 17 ndipo ndili Fomu 4. Ndili ndi chibwenzi chomwe ndakhala nacho miyezi 6 ndipo timakondana kwambiri ngakhale anthu amayesetsa kuti tidane poimba foni ndi kutumiza mauthenga a pafoni zammanja (SMS) pamene sindili naye limodzi. Mnzangayu adayamba wanenapo zogonana kamodzi koma ndinakana ndiye kuyambira pamenepo amati ndiye kuti ndili ndi chibwenzi china chomwe ndimagonana nacho. Ngakhale zili choncho timakondanabe; sanasinthe chikondi chake pa ine ngakhale amalimbikira kunena kuti ndili wina mpaka timafika poyambana. Agogo, nditani kuti asiye kundiganizira zimenezi? Mwana wanga, Ndasangalala kwambiri chifukwa chondilembera kupempha nzeru kuti ndikuthandize kuti bwenzi lakolo lisiye kukukaikira za chibwenzi china. Choyamba ndikuthokoz kwambiri kuti bwenzi lakolo litakuuza zogonana iwe udakana kugonjera chilakolako cha thupi. Apo wadya 10 pa 10. Umenewo ndiye umunthu, mwana wanga. Atsikana ambiri amsinkhu wako agwa mmavuto aakulu chifukwa chovomereza kugonana ali pachibwenzi. Zimachitika ndi zambiri mukamagonana nthawi yoteero isanakwanekutenga mimba, kutenga matenda opatsirana kuphatikizapo Edzi, kulephera kupitirza sukulu ndi zina zotero. Zitakere ndiye kuti wadzionongera tsogolo lako. Ndiye iwe limbikira sukuluyo mpaka upite nayo patali; usalolere zogonanazo mpaka mutalowa mbanja. Ngati cholinga cha chibwenzi chanu nchoti mudzalowe mbanja, mwamuna wako adzakhala wosangalala kwambiri kuti iwe unali wodzisunga kufikira pomwe walowa mbanja. Ukadzangomuvulira ameneyo muli pachibwenzi sadzakhalanso nawe ndi chidwi, ndikuuze. Adzakhala kuti wathana nawe basi ndipo mathero ake adzakusiya. Ndithudi, mtima umenewo usausiye, mwanawe, ndipo kutsogolo udzasimba lokoma! Akuti Ndimusiye Anatchereza, Ndithandizeni. Ndili ndi chibwenzi chomwe chimafunitsitsa banja ndipo ndinavomera zochitenga. Koma poyamba mnzanga ndiye adandifunsirira ndiye pano mnzanga yemweyo akuti mkaziyo ngwachisawawa pomwe poyamba nditamufunsa adati ndi mkazi wabwino. Pano akuti ndimusiye ndipo ndikatenge tanga tonse kwa mkaziyo. Nditani pamenepa? ABWAM, Chiradzulu ABWAM, Chibwenzi sachita kufunsirirana. Inu vuto lanu ndi chiyani kuti mnzanu ndiye azichita kukupezerani mkazi wachibwenzi? Chimene chachitika apa ndi chinyengo basi. Mnzanuyo wakuyendani njomba ndipo sindikukaika kuti wayamba kudyerera maso pa mkaziyo. Naye akumufunanso nchifukwa chake akuti umusiye ndipo ukatenge katundu wako. Koma mwina nditafunsako, kodi inu ndi mkaziyo mudaonanapo nkuchezerana? Mwakhala pachibwenzi nthawi yaitali bwanji? Inu maganizo anu pa mpaziyo ndi otani? Mnzanuyo akamati mkaziyo ngwachisawawa, akutanthauza chiyani? Zili ndi inu kufufuza kuti mudziwe zoona zake za mkazi muli naye pachibwenziyu musanathamange zothetsa chibwenzi chanu chifukwa mwina payenda dumbo ndi kaduka pamenepa. Nthawi zambiri vuto lotuma mnzako kuti akufunire mkazi kapena mwamuna limakhala ngati limeneli. Mudziwa bwanji kuti pofunsirana kuseriko akukhuthulanso zakukhosi kwawo? Dziwani kuti fumbi ndiwe mwini. +Evance Masina: Mapanga awiri samuvumbwitsa Pali mwambi woti ndigwire uku ndi uku pusi anagwa chagada. Penanso amati mapanga awiri avumbwitsa, kutanthauza kuti ndibwino kuchita chinthu chimodzi panthawi imodzi kuti zikuyendere. Koma Evance Masina akutha bwanji sukulu ndi kusewera mpira mkalabu komanso nkumachita bwino mzonse? DAILES BANDA adacheza naye motere: Akufunitsitsa atadzasewerapo kunja Ndikudziwe mnyamata. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ndine Evance Masina wa zaka 18. Ndimachokera mmudzi mwa Ntamba T/A Nkalo mboma la Chiradzulu. Ndine wachinayi mbanja la ana asanu. Pakadalipano ndikuphunzira pasekondale ya Moyale ku Mzuzu komwe ndili mu Fomu 3. +Umatchuka kwambiri chifukwa chosewera mpira, kodi udayamba bwanji kusewera? Mpira ndidayamba kalekale ndili mwana koma zenizeni ndidayamba kusewera wa Under-12. Ndinkasewera timu ya Young Buffalo ya ku Mzuzu konkuno. Nditadutsa zaka 12 ndidapitiriza kusewera ku Young Buffalo mtimu ya Under-14. Padachitika zovuta zinazake zomwe zidandichititsa kuti ndikayambe kusewera ku Chiputula United mtimu ya Under-20. Mchaka cha 2014 ndi pomwe ndidayamba kusewera mutimu ya Fish Eagles komwe ndili mpaka pano. Timuyi ikutsogola muligi ya chikho cha FMB ku Mzuzu kuno ndi mapointi 38. +Wachinyako zigoli zingati kutimiyu? Ndachinya zigoli 26 mumasewero okwana 14 mchikho chimenechi. +Chisangalalo chako ndi chotani pokhala amene wachinya zigoli zambiri mligiyi? Ndine wosangalala kwambiri chifukwa si chinthu chapafupi kuchita zoterezi. Pokhala mwana wasukulu zochita zimandichulukira. Ichi ndi chinthu chomwe ndakhala ndikufuna nditakwaniritsa mmoyo mwanga ndipo ndine wokondwa kuti ndachikwaniritsa. +Umakwaniritsa bwanji kupanga za sukulu ndi za mpira? Ndimayesetsa kupanga pulani momwe ndichitire tsiku ndi tsiku ndi cholinga choti ndizitsatira bwinobwino zomwe ndikufunika kuchita kupewa kusokoneza zochita zina. +Masomphenya ako? Chachikulu chomwe ndimafuna nditakwaniritsa ndi kusewera mutimu yaikulu mMalawi muno monga Silver Strikers, komanso mutimu ya dziko. Ndimafunitsitsanso nditadzasewerako mutimu yakunja. +Osewera amene amakusangalatsa ndi ati? Ndimasangalatsidwa ndi maseweredwe a Chawanangwa Kaonga wa timu ya Silver Strikers komanso James Rodriguez amene amasewera mutimu ya Real Madrid. +Umakonda kuchita chiyani ukakhala sukusewera mpira? Ndimakonda kuonerera mafilimu ndi kumvetsera nyimbo. +Achinyamata anzako uwalangiza zotani? Alimbikire pachilichonse kuti adzakhale opambana. +Mikangano ya mafumu yankitsa Ngakhale pali mkangano pakati pa maanja awiri wokhudzana ndi ufumu a Kapoloma ku Machinga, boma lati silibwerera mmbuyo pankhani yokalonga ufumuwu. +Mneneri wa unduna wa maboma angonoangono Muhlabase Mughogho adati boma ndilomangika manja ndi chigamulo cha khoti ndipo lipitirira ndi kulonga ufumuwo Loweruka pa 6 December 2014. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Khoti lidagamula kuti Ahmed Gowelo ndiye woyenera kulowa ufumuwo ndiye ife kuti tisalonge tiputa mlandu osatsata chigamulo cha khoti, adatero Mughogho. +Chikalata cha mbiri ya ufumuwu chimasonyeza kuti ufumuwu umayendetsedwa ndi maanja awiri molandirana koma zinthu zidavuta mchaka cha 2007 yemwe adali mfumu pa nthawiyo atamwalira. +Mkangano wina udabuka ku Zomba wolimbirana ufumu wa Malemia koma Mughogho adati mkanganowu ukuwunikidwa kubwalo la milandu choncho mpovuta kulankhulapo. +Mkangano wa ufumu wa Malemia ndiwovuta koma padakalipano uli kubwalo la milandu ndiye sitinganenepo kanthu mpakana bwalolo litagamula, adatero Mughogho. +Undunawu udalinso ndi mkangano wa ufumu wa Mduwa ku Mchinji koma Mughogho adati mkangano uwunso udagamulidwa kukhoti. +Petros Chitedze mmodzi mwa akuluakulu omwe amatsata za ufumuwo adati mkanganowo udakalipo. +Kumeneko, Patson Magaleta wa banja la Magaleta akulimbirana ufumu wa Mduwa ndi Andrew Patrick Mderu mdzukulu wa Mduwa. +Mughogho adati pofuna kuthana ndi mapokoso oterewa, unduna udakhazikitsa komiti yoti izigwira ntchito ndi mafumu ndi ma DC posankha woyenera kulowa ufumu. +Iye adati mikanganoyi imayamba kaamba kosungitsana ufumu wina akamwalira komanso kuyambitsa midzi ingonoingono yomwe boma silikudziwa. +Tidapempha DC kuti mfumu ikamwalira ndipo wina nkulowapo ngati wongogwirizira, asamamulole kuchita nawo misonkhano chifukwa oterewa akaona zokoma za ufumuwo ndiwo amayambitsa zokakamira eni ake akati autenge, adatero Mughogho. +Alimi avale dzilimbe, kukubwera El Nino Akatswiri a zanyengo alosera kuti chaka chino pali mantha kuti dziko lino lingakumane ndi nyengo yoipa ya El Nino. +Lipoti la BBC lomwe alitulutsa posachedwapa, zofufuza za ofesi yoona za nyengo ya United Kingdom Met Office zikuonetsa kuti zaka ziwiri zikubwerazi kukhala nyengo yotentha koopsa padziko lonse, zomwe zingapangitse kusintha kwakukulu pa mmene nyengo imakhalira. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Nalo bungwe loona za mavuto a njala kummwera kwa kwa Africa la Famine Early Warning Systems (Fews-Net) lati mmene zikuonekera nyengo ya El Nino iyamba mosapeneka October mpaka December. +Tikati tione mmene zakhala zikuchitikira mmbuyo, kukakhala El Nio mvula simagwa mmene anthu amayembekezera ndipo ati chaka chino zigawo za kummwera kwa Mozambique, Malawi ndi Zimbabwe mvula itha kuvutiraponso monga zidachitikira mu 2014/15. +Nyengoyi ikudza pamene chaka chino alimi ambiri mdziko lino akulira chifukwa cha kuchepa kwa mvula, pamene ena mvula idangogwa yochuluka kwa nthawi yochepa ndipo mbewu zawo zidakokoloka. +Kukakhala El Nino mwina mvula imagwa mosadukiza komanso ikadula mwina kumakhala ngamba kwa nthawi yaitali, zomwe zimakhudza kwambiri alimi. +Mnyengo zovuta ngati zimenezi, ndi alimi okhawo otsata bwino ndondomeko zamalimidwe amene amapezabe phindu paulimi wawo kukakhala El Nino. +Prof. Moses Kwapata wa kusukulu ya zamalimidwe ya Luanar ku Lilongwe akuti zateremu alimi asagone koma ayambiretu kukonzekera ulimi wa chaka chino. +Ngati sadamalize kusosa akuyenera apange changu ndipo agalauziretu minda yawo. Zikatere pamafunika kuti mvula yoyamba ikamagwa zonse zakumunda zikhale zatha kuti alimi athe kubzala ndi mvula yoyambirira, adatero Kwapata pouza Uchikumbe. +Feteleza aguliretu, ndipo adzaonetsetse kuti amuthira panthawi yake. Ngati mmunda mwamera tchire asachedwetse kupalira. Chilichonse chikhale mchimake. Mlimi wotere ngakhale nyengo yavuta ndiye amene amakolola. +Kwapata adati ngati mwayi ali nawo alimi akuyeneranso kulima mbewu zosiyanasiyana chifukwa zina zimafuna mvula yambiri pomwe zina sizikonda mvula yochuluka. +Malawi sisewera ndi Uganda Chiyembekezo chidalipo kuti Malawi iswana ndi Uganda kuti ikonzekere masewero a World Cup pa 7 October pamene ikunthane ndi Tanzania. +Koma mlembi wa bungwe loyendetsa masewero mdziko muno la FAM, Suzgo Nyirenda, walengeza kuti izi sizithekanso chifukwa osewera a Flames amene amasewera mpira wawo kunja kwa dziko lino sakwanitsa kudzasewera masewerowo chifukwa makalabu awo akhala otangwanika. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Malinga ndi Nyirenda, Flames idzanyamuka mdziko muno ulendo ku Tanzania pa 4 October osachita zokonzekera ndi timu iliyonse. +Koma kochi wa timuyi, Ernest Mtawali, pofuna kupima mphamvu za anyamata ake, adakonza masewero ndi FISD Wizards Lachitatu ndipo Flames idapambana 4-0. +Flames idzakumananso ndi Tanzania pamasewero achibwereza pa 11 October pa Kamuzu Stadium mumzinda wa Blantyre. +Zig Zero: Mnyamata wa nyimbo za dansi Kuyambira kuubwana wake chimene amaganiza, kulota ndi kuchita ndi kuimba nyimbo basi. Inde, Mulungu adamudalitsa ndi liwu lanthetemya mnyamata ameneyu ndipo pano akugwiritsa ntchito luntha lomwelo kuti apeze chakudya cha tsiku ndi tsiku komanso zosowa pamoyo wake. Uyu ndi Joseph Alufandika, mnyamata wosangalatsa anthu ndi mingoli yokoma. CHIMWEMWE SEFASI adapezana naye poduka mphepo ndipo adacheza naye motere: Kudyera pakamwa: Alufandika Ndikudziwe Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Dzina langa ndine Joseph Alufandika, ndipo ndine wosakwatira, ndimachokera kuchigawo chakumwera konkuno mboma la Nsanje. Anthu okonda nyimbo za dansi amandidziwa ndi dzina loti Zig Zero. +Kodi kuimba nyimbo za dansi udayamba liti? Kuimba ndidayamba pakale ndithu. Ndili kusekondale ndi pamene ndidazindikira kuti ndili ndi luso losangalatsa anthu kudzera mumaimbidwe, munyimbo za dansi. +Kodi kupatula kuimba umachitanso chiyani? Inetu ndimapanga bizinesi komanso ndikupitiriza maphunziro kusukulu ya Malawi College of Accountancy komwe ndikuphunzira zoonkhetsa chuma. +Kodi chimbale chako chatsopano chituluka liti? Mutu wake ndi chiyani? Chimbale changa chikuyembezereka kutuka kumapeto a mwezi wa August, chomwe chikhale ndi nyimbo 14 zomwe zaimbidwa mChichewa ndi mChingerezi. Ndipo kuyambira pa 3 August mpomwe nditawadziwitse Amalawi zambiri. +Kodi ndi mavuto ati omwe oimba nyimbo za dansinu mumakumana nawo? Mavuto omwe timakumana nawo ndi monga kupita kuzoimbaimba koma osapatsidwa ndalama yomwe tinagwiriza. Kumeneku ife timaona ngati tikuponderezedwa komanso anthu ena kuti atukule luso lathu amafuna kuti tiwapatse ndalama. +Kodi nyimbo za dansi ngati zomwe umaimba iweyo ukuona kuti zikupita patsogolo? Kunena mosanama, Chimwemwe uli apa, nyimbo zaimbidwa ndi achinyamata zikupita patsogolo kwambiri chifukwa anthu akati ali pamalo achisangalalo monga kuukwati, zinkhoswe, malo osiyanasiyana, chisangalalo chawo chimakhala chopambana chifukwa cha uthenga womwe tikumapereka kudzera mnyimbo zomwe tikumawapatsira . +Kodi ndi anthu ati omwe unaimbapo nawo nyimbo limodzi chiyambireni kuimba pa Malawi pano? Inetu chiyambireni kuyimba pa Malawi pano ndaimbapo nyimbo ndi anthu ambiri monga Marcus Pasanje wa Dare Devils, Blasto, BFB ndi ena ambiri. +Pomaliza tandiuze zomwe umakonda. +Ine ndimakonda kuimba ndi kumvera nyimbo. Nthawi zina ndimakonda kuyenda ndi kumaona malo osiyanasiyana ndi kukumana ndi anthu osiyanasiyananso. +Mdima wanyanya mmakhonsolo Zomwe anena a makhonsolo a mizinda ya Lilongwe Blantyre ndi Mzuzu zikusonyeza kuti vuto la mdima mmisewu ya mizindayi litenga nthawi kuti lithe kaamba koti, ngakhale akuyesetsa kuti akonze zinthu, anthu ena akubwezeretsa zinthu mmbuyo poononga dala zipangizo za magetsi. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Escom in free-for-all fuel scam Khonsolo ya mzinda wa Lilongwe yati vuto lalikulu ndi nthawi yomwe kampani ya magetsi ya Escom imatenga kuti ikalumikize magetsi ntchito yozika mapolo ikatha. +Mneneri wa khonsoloyi, Tamala Chafunya, wati khonsolo ikamaliza kuzika mapolo nkulumikiza nthambo za magetsi, zimakhala mmanja mwa Escom kuti idzamalizitse ntchitoyo polumikiza magetsiwo. +Gawo lathu pa ntchito imeneyo idachitika ndipo kuchedwaku ndi kampani ya Escom. Khonsolo idalipira kale ndalama zolumikizira magetsi koma zaka zikungopita ngakhale kuti timayesetsa kutokosako, adatero Chafunya pouza Tamvani pa nkhani ya vuto la mdima mmisewu yambiri mumzindawu. +Chafunya adati kuchedwaku kumapereka danga kwa anthu amaganizo olakwika kuti aziononga mapolowo ndipo chipsinjo chimagweranso pamsana pa khonsolo kukonzanso mapolowo. +Mneneri wa kampani ya Escom Kitty Chingota adavomereza kuti khonsoloyi idalipiradi ndalama zolumikizira magetsi koma akatswiri ake atakayendera malo ofunika kulumikiza magetsiwo adapeza zolakwika zambiri. +Iye adati pofuna kupewa ngozi za magetsi, kampaniyi idalangiza khonsoloyi kuti ikonze molakwikamo magetsewo asadabwere koma palibe chomwe achitapo. +Mmalo ena mapolo adadutsa mmunsi mwenimweni mwa nthambo zathu za magetsi ndipo malamulo a Escom salola kulumikiza magetsi mmalo oterewa. Mmalo ena mapolo adatalikirana kwambiri chifukwa ena adagwetsedwa ndi anthu opotoka maganizo ndiye mpovuta kulumikiza magetsi mmalo oterewa, adatero Chingota. +Koma Chafunya adati nthawi zambiri mapolowo akawonongedwa kumakhala kovuta kuwabwezeretsa chifukwa ndalama zomwe zimalowa nzochuluka kwambiri. +Kukonza polo ya simenti imodzi yokha, kuyambira kuwumba mpaka kukaizika, imatenga ndalama zokwana K400 000 ndiye muwerengere kuti msewu umodzi umadya ndalama zingati za mapolo, nanga anthu akawononga kuti tikabwezeretse ndiye kuti zitukuko zina ziimiratutu, adatero Chafunya. +Mumzinda wa Blantyre nkhani ndi yokhayokhayi; mmisewu yambiri ndi mdima wokhawokha kaamba koti mapolo ambiri adagwtsedwa ndi akuba, zomwe zikuchititsa kuti ena azichitidwa chipongwe chifukwa cha kusowa kwa kuwala usiku. +Mneneri wa khonsoloyi Anthony Kasunda adati nzoona kuti mumzindawu muli vuto la magetsi mmbali mwa misewu chifukwa ambanda adaba zipangizo pamapolo. +Ili ndi vuto lalikulu chifukwa anthu amayenda mwamantha usiku. Pamene khonsolo ikuyesetsa kuti ngati mzinda tipite patsogolo ndi chitukuko, anthu ena amaganizo olakwika akubwezeretsa chitukuko mmbuyo pomaba zipangizo ngati zothandizira magetsi a pansewu, adatero Kasunda. +Iye adati ngati khonsolo akupempha a makhoti kuti pamene munthu wagwidwa ndi katundu wa khonsolo, ameneyo azilandira chilango chokhwima kuti asadzabwerezenso, komanso kuti ena atengerepo phunziro. +Komanso tikufuna tipeze njira imene tingachite kuti zipangizo za magetsi zisamabedwe monga pogwiritsa ntchito magetsi oyendera mphamva ya dzuwa ija pa Chingerezi amati solar powered system. +Pempho lathu ngati khonsolo ndilakuti tiyeni tonse titengepo gawo poteteza katundu kapena zipangizo zimene khonsolo imaika mmalo osiyanasiyana kuti zitumikire anthu okhala mumzinda wa Blantyre. Isakhale ntchito ya khonsolo yokha koma tonse, adatero Kasunda. +Namonso mumzinda wa Mzuzu nyimbo ndi yokhayokhayoambanda ali kaliriki kuononga zida za magetsi mmbali mwa misewu moti malo ambiri mdima uli bii usiku ukagwa. +Zinthu zidayamba kusonya pamene magetsi oyamba mmisewu ya mmataunishipi monga Zolozolo, Chimaliro, Katawa ndi Msongwe adayatsidwa mu 2012 ndi 2013, koma pano zinthu zabwerera mmbuyo chifukwa anthu ena adayamba kuba nthambo za magetsiwa. +Wogwirizira mpando wa mkulu wa khonsoloyi, Victor Masina, adati ili ndi vuto lalikulu ndithu moti pano a khonsoloyi akufuna ndalama zosachepera K3.5 miliyoni kuti akonzenso zipangizo zoonongekazo monga ma transformer ndi mapolo ogwetsedwa ndi galimoto zikaphuluza msewu. +K85 000 kapena chaka kundende atapha galu Ena amangopha agalu koma sapatsidwa chilango, koma khoti la Ulongwe Majisitireti ku Balaka lalamula kuti mfumu ina ilipe K85 000 apo ayi, ikakhale kundende chaka chimodzi kaamba kopha galu ndi kuwononga mmera mdimba la mkulu wina. +Malinga ndi mneneri wa polisi ya Balaka, Joseph Sauka, mfumuyi ndi Peter Kasanga koma dzina lake lenileni ndi Michael Mailosi, wa zaka 62. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Sauka adauza Tamvani msabatayi kuti nyakwawayi pa 19 March chaka chino idapezeka mdimba la Yona Nansambo ikuswa malambe. Poswapo akuti idawandanso chimanga cha mkuluyu. +Iye adati Nansambo atadzudzula mfumuyi kuti isiye zimene imachita mdimbamo, iyo idakula mtima ndipo idayamba kuthafulira mwini dimbali ndipo ndewu idabula pakati pa awiriwa. +Achibale 6 a mfumuwo akuti atamva kuti mfumuyi ikugogodana ndi munthu, adathamangira kudimbako komwe adakalowerera ndewuyo. +Bwalo la milandu lidamva kuti anthuwo sadalekere pomwepo koma adalonda mwini dimbayu kunyumba kwake komwe adakaswa galasi la galimoto komanso kupha galu, adatero Sauka. +Kubwaloko, anthuwa adakana za mlandu wopha chiweto malinga ndi gawo 343 la malamulo a dziko lino, komanso adakana mlandu wowononga galimoto malinga ndi gawo 344. Koma bwalo litabweretsa mboni, anthuwa adapezeka ndi mlandu. +Wapolisi woimira boma pamlanduwo, Sergeant Yohane Chaomba, adapempha bwalo kuti lithambitse mfumuyi ndi chilango chokhwima chifukwa monga mfumu sidaonetse chitsanzo chabwino. +Sauka adati mfumuyi idapempha bwalo kuti limumvere chisoni chifukwa ndi yokalamba komanso kuti mkazi wake akudwala. +Koma Third Grade Magistrate Peter Mkuzi adalamula mfumuyi kuti ilipe K60 000 powononga komanso K25 000 popha galu, apo ayi, akaseweze chaka kundende ndi kukagwira ntchito ya kalavula gaga. +Mkuzi adalamulanso abale asanu a mfumuyi kuti alipe K25 000 aliyense, apo ayi, akaseweze kundende miyezi isanu ndi inayi (9). +Omangidwa akuchokera mmudzi mwa Peter Kasonga, kwa T/A Kalembo mbomalo. Pofika Lachinayi pa 11 June nkuti anthuwa asadapereke chindapusacho. +Kumisasa kwabuka matenda a maso, mphere Nyumba zawo zudagwa, minda idakokoloka ndipo katundu wambiri kuphatikizapo ziweto zidanka ndi madzi osefukira. Anthu miyandamiyanda, maka akuchigwa cha Shire, adathawira kumtunda kuti apulumutse miyoyo yawo, koma komwe adathawirako nakonso kwaopsakwagwa mliri wa matenda amaso ndi mphere mmisasa ya ku Nsanje ndi Chikwawa. +Mneneri wa unduna wa zaumoyo Henry Chimbali watsimikiza izi, koma wati unduna wake ukufufuzabe za anthu amene akhudzidwa ndi matendawa. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Msasa wa Bitirinyu kwa T/A Nyachikadza mboma la Nsanje ndiwo wakhudzidwa kwambiri ndi matenda a mphere pamene misasa ya Bereu ndi Kalima kwa T/A Maseya mboma la Chikwawa ndiwo watekeseka ndi matenda a maso. Msasa wa Bitirinyu ukusunga anthu pafupifupi 6 000. +Pamene Tamvani idazungulira pamsasa wa Bereu ambiri adali koyenda koma mayi Elube Jeke wa mmudzi mwa Chikutireni adali pamalopo akutonthoza ana ake. +Mwana wamngonoyu wayamba kumene [kudwala maso] pamene wamkuluyu ndiye adayamba masiku atatu apitawo. Sakupeza bwino, maso atupa komanso akumadandaula kuti akumva kuwawa. +Akapeza mtendere ndiye kuti wagona. Sitinalandirepo thandizo chiyambireni matendawa, zomwe zachititsa kuti pakhale kupatsirana, adatero Jeke uku akufunditsa mwana wokulirapoyo amene ati sakupita kusukulu chifukwa cha mavutowo. +Mavuto sakukata kwa Jeke chifukwa pamene amabwera pamsasawo nkuti nyumba yake itagwa ndi madzi a mvula ndipo katundu wake limodzi ndi munda zidakokoloka. +Poti athawitse moyo, lero wakumana nazonso pamene matenda agwera ana ake. Sindingakhalenso ndi lingaliro lobwerera kumudzi chifukwa kumenekonso ndiye sikuli bwino. Madzi sadaphwere, adatero Jeke, kusowa mtengo wogwira. +Mkulu woyanganira za umoyo pa msasawu, Rodrick Rivekwa, akutsimikiza za matendawa ndipo wati pofika Lachisanu pa 13 March nkuti anthu 15 atapezeka ndi matendawa. +Iye adatinso anthu 10 ndiwo apezeka ndi mphere pamsasawo. +Koma boma lachitapo machawi pofuna kuthana ndi vutoli. Adatitumizira mankhwala moti anthu onse amene akudwala maso ndi mphere alandira thandizo lachipatala, adatero Rivekwa. +Iye adati kuchulukana kwa anthu pamsasa wa Bereu lingakhale vuto lina lomwe ladzeetsa mavutowo. +Tili ndi anthu 1 024, koma malo ogona adali ochepa. Komanso kupeza madzi ndi aukhondo lidali vuto lina. Panopa bolako chifukwa atipatsa zipangizo zosungiramo madzi komanso matenti adationjezera, adatero Rivekwa. +Nakonso kumsasa wa Kalima mavuto a matenda amaso sadasiye, malinga ndi John Yobe wa mmudzi mwa Kalima kwa T/A Maseya mbomalo. +Yobe adathawa mmudzi mwake ndi kukakhala nawo kumsasawo. Iye akuti adali ndi ziweto monga nkhuku, mbuzi ndi nkhumba zomwe zidatengedwa ndi madzi. +Pokakhala pamsasawu akuti amati ndi chisomo ndipo ankaganiza kuti wapulumuka, koma mwadzidzidzi adadabwa kuona ana ake asanu ndi mmodzi atagwidwa ndi nthenda ya maso. +Yobe akuti pano zinthu zasinthako chifukwa thandizo la chipatala lidafika mofulumira ndipo nthendayi ati sidafale kwambiri monga amaopera. +Malinga ndi nyakwawa Katandika, matendawa adza chifukwa chothithikana pamsasawu, zomwe anthuwa akhala akudandaula. +Koma Chimbali adati unduna wake wafika kale mmalowa kukapereka thandizo la chipatala ndipo zinthu zikusintha. +Talandiradi malipoti okhudza matenda a maso. Ambiri amene akhudzidwa ndi matendawa ndi ana. Msasa wa Bitirinyu kwa T/A Nyachikadza ndiko talandira malipotiwa. Koma zinthu zasintha chifukwa thandizo lapitako, adatero Chimbali. +Iye adatinso mavutowa amveka mmaboma a Chikwawa ndi Nsanje kokha pamene mmaboma ena monga Thyolo ndi Mulanje komanso ku Balaka kulibe nkhaniyo. +Mneneriyo adatinso matenda otsekula mmimba abukanso mmisasayi koma unduna wawo wapereka kale thandizo. +DPP, Kasambara trade barbs, witnesses scared There was drama in the High Court in Lilongwe yesterday when a former student and her lecturer locked horns across the divide of the prosecution and defence in the ongoing Paul Mphwiyo shooting trial. +Private practice lawyer and accused person Ralph Kasambara and Director of Public Prosecutions (DPP) Mary Kachale exchanged tough words, with the former minister of Justice and Constitutional Affairs accusing the prosecution of personal persecution. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Kachale (L): The allegations are far from the truth Kasambara belittled Kachales concerns that he and other accused persons had intimidated State witnesses who, she said, fear for their lives. But Kasambara said the DPP was just being dramatic. +Said Kasambara: The drama being played by the DPP is obvious. She knew she was dealing with elusive witnesses. All this is for dramatic effect to castigate us. All this is intended to play with the public and the media, all just to attack me. +He alleged that a police officer from Blantyre, Alex Phiri, had been making night phone calls threatening his wife and brother-in-law with prosecution if they did not comply to testifying against the senior counsel, but Kachale vehemently denied the allegations. +Kasambara during an earlier court appearance Kasambara further accused Kachale of favouring another accused person, Oswald Lutepo, who is not subject of bail revocation. +She shot back that as her former boss and trainer, she had a lot of respect for Kasambara; hence, she could not have a personal vendetta against him. +This [prosecuting Kasambara] was not an easy decision for me to take, but I took it. The allegations he is making here are far from the truth. We do not intend, as the State, to call his wife as a State witness. These serious allegations are casting a slur on my character as well, Kachale charged back. +On allegations of favouring Lutepo, Kachale said if he were her favourite, she would not have added him to the case once she examined the evidence and affidavits when she came into the office of the DPP. +Kachale insisted that the prosecution had evidence to show witness tampering, but in the meantime, they would ask the court to subpoena them to appear in court by force even though they might become hostile witnesses. +Another defence lawyer, John-Gift Mwakhwawa, intervened in the heated exchange and recommended that the State should use the machinery at its disposal to bring the State witnesses to court. +Earlier, the DPP told the court that State witnesses were not willing to testify against the six accused persons, claiming that they fear for their lives. +Some of the witnesses have been given police protection, but they said they are still afraid to testify against Kasambara, Macdonald Kumwembe and Pika Manondo who are answering charges of attempted murder and conspiracy to commit murder. +Kachale said she was forced to ask for an adjournment after the witnesses lined up to testify, including a Chalunda and Defeneya, a ballistics expert from the Malawi Police Service, a police investigator and officials from Airtel Malawi who have since been withdrawn as witnesses. +Chalunda and Defeneya approached the prosecution and recorded statements in which they made allegations of intimidation from the accused persons only to change tact and claim that the prosecution was forcing them to change witness statements. +She added that the prosecution had concrete evidence to show the level of intimidation the witnesses have undergone. +Presiding High Court judge Michael Mtambo is yet to make a ruling on an application to revoke bail for the accused persons who she accused of engaging in mafia-like operations to intimidate witnesses and prevent them from testifying against them. +The other accused persons are Dauka Manondo, Lutepo and Robert Kadzuwa whose bail has since been revoked for failing to show up for trial for two consecutive sessions. +Msoliza, Kayuni share spoils Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ernest Msoliza and Osgood Kayuni fought to a draw in an eight-round welterweight bout at Obrigado Leisure Centre in Mzuzu on Saturday. +The Mzuzu-based boxer Msoliza failed to make use of home advantage against Kayuni who had an upper hand in the first three rounds. +Osgood Kayuni Backed by home support, Msoliza upped the tempo in the fourth round with a flurry of punches, but his seasoned opponent held. +Following Saturdays bout, Kayuni now has a record of 30 fights with 22 wins, lost five and three draws. +On the other hand, Msoliza has 11 fights with seven wins, two losses and two draws. +Speaking after the bout, Msoliza claimed he was robbed of victory The bout was good, but I am not happy with the results, I dominated most of the rounds, but I am surprised that the judges have settled for a draw. I have been robbed of victory, said Msosliza. +Msoliza Surprisingly, Kayuni also claimed to have been robbed. +I have been hearing that judges here favour Mzuzu-based boxers and I have proved it today. I just cant understand how they settled for a draw, this is not good for the sport, lamented Kayuni. +In supporting bouts, Laston Kayira beat Alexander Likande while Lomelu Mwakhwawa beat Wilfred Nyambose. Ruth Chisale defeated Violet Nyambose. +Joe Nyirongo who promoted the fights, said he was impressed with the performance and pledged to continue organising bouts in the city. +The fights went on well. I am happy with the results. I feel judges have the mandate to rule who has carried the day. I promise to continue supporting boxing. I am here to stay. I want to make sure that I assist the government in putting Malawian boxers on the global map, said Nyirongo. +Mzuzu district sports officer Olga Mshali said her office will make sure that boxing is supported just like any other sporting activity in the city. She then appealed to the corporate world to emulate what Nyirongo is doing in supporting boxing. +Katelele back in the studio Sensational musician Katelele Chingoma is back in the studios where he is recording a new album that is expected to hit the market in May. +The musician, fondly known for composing reggae and Sena jive songs, has recorded nine of 10 songs to be roped into the album, Zanga Zatheka. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Her touch on murals Katelele: The songs have been recorded at a number of studios As usual, the artist has used his brother Petros, a versatile producer, on the consoles. +I have used my brother again this time because he understands the type of music my fans like. The songs have been recorded at a number of studios in Lilongwe and South Africa and this will bring about a mixed blend. I deliberately did this to make sure that I come up with the best quality music that will soothe my fans, said the Blantyre-based musician. +The musician, famed for the track Asowe Mlamu, said his trip to South Africa late last year has helped him to tap more skills from SA musicians. +I went there and conducted live shows with Thomas Chibade and Moses Makawa. I utilised my trip to tap more talent from artists such as DJ Cleo, with whom I shared the stage. I hope the fusion of talent will help my album sell well locally and internationally, said the musician. +Katelele released his album Ndili Nawo Mwayi in 2011 and says he has taken time preparing for the new album. +I feel bad if fans dont welcome my music. That is why I dont rush in releasing albums. I want to stand to quality; hence, my four-year silence. I hope the album will sell well considering that I have taken a lot of time to prepare, said the musician. +Katelele says he will work with reggae outfit Black Missionaries to promote the album once it gets on the market. +Kusanthula gule wa likwata Likwata ndi mmodzi mwa magule amene amavinidwa pakati pa Ayao. Ndidali mboma la Chiradzulu mmudzi mwa Njeremba kwa T/A Mpama komwe adapezerera gule wa likwata, yemwe ena amamutcha kuti namkwakwala. Uyutu ndi gule amene amavina amayi komanso atsikana. Kodi uyu ndi gule wanji? Nanga adayamba liti? Mtolankhani wathuyu adakokera pambali mayi amene amatsogolera guleyu. Adacheza motere: Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Eee! Wefuwefu ameneyu kutopa kumene? Hahaha! Padalitu ntchito pamene paja. Si maseweratu kuvina gule ameneyu chifukwa akafika pakolasi timayenera tidzipinde basi. +Tidziwane kaye. +Ndine mayi Idesi Chiwaya, ndipo ndipo ndimatsogolera gululi. +Kodi ndi gule wanji ameneyu? Ameneyu ndi gule wa namkwakwala, ena amati likwata. +Cholinga cha guleyu nchiyani? Kusangalatsa anthu basi. Timavina tikasangalala monga zachitikira leromu kuti tangosangalala ndiye tidakumana kuti tivine basi anthu adyetse maso. +Muli akazi okhaokha bwanji? Ameneyu ndi gule wa amayi, nchifukwa chake simudaonemo mwamuna kupatula awiri amene akutiimbira ngoma. +Ndaonamonso tiasungwana, timeneti timaloledwanso kukhala mgulumu? Eya, amenewo ndiye eni gululi chifukwa ife takulatu ndiye timakhala nawo kuti Mulungu akatitenga iwowo ndiwo adzatsogolere gululi. Sitikufuna kuti gule ameneyu adzafe. +Kodi guleyu saphunzitsa zoipa? Zoipa zanji? Ayi, ameneyutu ntchito yake ndi kusangalatsa anthu basi. +Simukuona kuti guleyu angapangitse kuti tianamwali tija tisodzedwe mwachangu? Hahaha! Musandiseketse inu, amene aja ndi adzukulu anga. Ndimawayanganira ndipo palibe angachite zopusa ndi ana amenewa. Akukula mmanja mwanga. +Dzina limeneli lidabwera bwanji? Dzina la guleli? Liti lomwe mukukamba? Ndikukamba la likwata Ndi dzina basi, kusonyeza gule wachikhalidwe pamene ena amati gule wa namkwakwala. +Chifukwa chiyani kulipatsa dzina la likwata? Basi, nawonso makolo adakonda kuti apereke dzinali. +Si zolaula zimenezi? Nanga mpaka likwata? Ayi, palitu maina a anthu ambirimbiri mdziko muno omveka ngati akulaulanso, kodi ndiye kuti anthuwo amachita zomwe dzinalo limatanthauza? Ife mukanena kuti likwata timatanthauza kuti ndi gule wosangalatsa basi. +Kodi ndi gule wa chikhalidwe chiti cha anthu? Uyu ndi gule wa Anyanja. Ambiri akhala akunena kuti ndi wa Alhomwe, koma zoona zenizeni ndi zomwe ndikunenazi. +Mavinidwe a guleyu andimaliza, tafotokozani momwe muchitira pamene mukuvina Ngoma ija ikamalira, ife timavina moitsatira uko tikuimba nyimbo zathu. Ndiye ikafika pakolasi, timachita ngati tikudumpha uko tikudula chiuno. Apa ndiye timagwadirira pansi ndi kuvina momatembenuka koma kumatembenuka ndi maondo kwinaku tikugundana ndi matako. Aka ndiye kavinidwe kake. +Adakuphunzitsani ndani? Makolo athu. Ineyo makolo anga ankavina kwambiri ndipo atamwalira ndidapitiriza mpaka kupeza amayi anzanga. Tonse tilipo 10 kuphatikizapo ndi abambo a ngoma takwana 12. +Abambo savina nawo chifukwa chiyani? Aaa! Inuyo mungakwanitse zomwe timachita zija? Eetu, nchifukwa timavina amayi okha. +Mudayamba liti kuvina guleyu? Chaka ndiye sindingakumbuke koma ndimakumbukira kuti panthawiyo ndidali ndi zaka 33. Pano zaka zanga ndidaziiwala koma zaposa 50. +Mumavina nthawi yanji? Timavina masana, moti nthawi zambiri timavina pazochitika monga pamisonkhano. Tavinirapo mtsogoleri wakale Bakili Muluzi komanso Bingu wa Mutharika. +Atsogoleriwa amakwanitsa kuduka mchiuno chonchi? Ayi, amangochoka pampando ndi kumavina pangonopangono ndipo mapeto ake amapisa mthumba kutipatsa kangachepe. +Kodi momwe munavinira apamu ndiye kuti mumathera pamenepa? Ayi, apatu tangovina kwa mphindi 5, koma tikati tivine moposera mphindi zimenezi mudakaona momwe timachitira. +Malangizo kwa amene satsatira gule wa makolo Amenewo azikhala pafupi ndi makolo awo kuti asataye chikhalidwe cha makolo awo. +Ulangizi wa pafoni uthandiza alimi Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ndizachidziwikile kuti dziko la Malawi limadalira ulimi pa chuma chake ndipo ambiri mwa alimi mdziko muno ndi alimi a minda ingonoingono omwe amadalira alangizi kuti awafikire ndi njira komanso luso la makono pa ulimi. +Nawonso akatswiri a za ulimi omwe akukangalika kuchita kafukufuku pofuna kupeza njira komanso luso la makono paulimi amadaliranso alangizi kuti afikire alimi ndi luso ndi njira za makonozi. +Koma ngakhale izi zili choncho, ntchito za ulangizi zikukumana ndi mavuto ochuluka monga mlili wa Edzi, kuchepa kwa zipangizo zogwiritsa ntchito, ufulu pankhani za misika komanso ufulu wa demokalase kungotchulapo ochepa. Kupatula zonsezi, onse okhuzidwa ndi ntchito za ulangizi akhala akutsatira njira za ulangizi zodalira kuti mlimi ndi mlangizi akumane maso ndi maso. +Pofuna kuchepetsa ena mwa mavutowa polingaliranso kuti chiwerengero cha alangizi chikuchepa, unduna wamalimidwe kudzera ku nthambi ya ulangizi mogwirizana ndi mabungwe omwe siaboma, adakonza msonkhano wokambirana zolimbikitsa ulangizi pogwiritsa ntchito luso lamakono pogwiritsa ntchito malo oimbira foni kapena kuunguza zinthu pa Internet. +Msonkhanowu udachitikira ku Malawi Institute of Management mumzinda wa Lilongwe ndipo udabweretsa pamodzi akatswiri kuchokera ku unduna wa zamalimidwe, sukulu za ukachenjede za Luanar komanso NRC ndi makampani komanso mabungwe a Self-Help Africa, TNM, Airtel, Farm Radio Trust, Technobrain, atolankhani, alimi komanso ena ambiri. +Zolinga za msonkhanowu zidali zitatu. Cholinga choyamba chidali kukhazikitsa masomphenya a kayendetsedwe ka malo olandira ndi kupereka mauthenga a ulangizi (call centre). Chachiwiri chidali kugawana nzeru pakayendetsedwe ka malowa. +Chomaliza chidali kupangana momwe dongosolo la malowa liyendere kuno ku Malawi. +Akatswiri osiyanasiyana adapereka maganizo awo pakayendetsedwe ka malo amenewa. +Call centre ndi malo omwe alimi amene ali ndi foni za mmanja amatha kuimba kapena kutumiza mauthenga kufuna kupeza ulangizi ndipo akatero amalandira mayankho malingana ndi zomwe adafunsa. +Yemwe adatsogolera kupereka maganizo ake adali mkulu wa kampani ya foni za mmanja ya Airtel. Atatha mkulu wa Airtel, padabwera anthu asanu ndi awiri omwe adaperekanso maganizo awo motsatizana. +Anthu adaloledwa kufunsa mafunso ndi kupereka ndemanga pa zomwe akuluakuluwa adalankhula. +Pamapeto pa zokambirana, anthu onse adagwirizana kuti njira yogwiritsa ntchito malowa yingathandize kwambiri kupereka ulangizi kwa alimi makamaka pano pomwe chiwerengero cha alimi chikuchuluka kuyerekeza ndi alangizi. +Pali chiyembekezo choti malowa athandiza kutukula nchito za ulimi popereka ulangizi woyenera panthawi yake. +Ndipo poyankhula pa mwambowu, mmodzi mwa akuluakulu mu unduna wa za malimidwe yemwenso adali mlendo wolemekezeka pa mwambowu Dr Wilfred Lipita adati iye akukhulupilira kuti umphawi ukupita mtsogolo pakati pa alimi kaamba kosowa uthenga wokwanira ndipo podzindikira kufunikira kogwiritsa ntchito njira zamakono pa ulangizi, unduna wake wakhazikitsa komiti yapadera yoonetsetsa kuti luso lamakono likugwiritsidwa ntchito bwino pa ulangizi yotchedwa the National Agricultural Content Committee for ICT. +Ngati unduna, tikudzindikira kufunikira kogwiritsa ntchito luso lamakono pa ulangizi kotero takhazikitsa komiti yapadera yoonetsetsa kuti pasakhale chisawawa pogwiritsa ntchito luso lamakono pa ulangizi,adatero Lipita. +Ngati muli ndi mafunso kapena ndemanga pa nkhaniyi, lemberani kalata kapena kuimba lamya kwa: Head Extension Department P. O. Box 219 Lilongwe 01 277 260. +Mlenje wakhapa mlimi ku Dedza Mlenje wina wa mmudzi mwa Mbwindi mdera la Mfumu Kachere ku Dedza wavulaza mlimi wa mmudzi mwa Kuchikowa pamene nkhwangwa yomwe adaponya kuti ilase nkhwali itaphuluza nkumulasa pa mutu. +Mlenjeyo, a Francisco Kwenda ndi mlimiyo, a Nachimwani Langisi, adalawirira aliyense kukagwira ntchito yake. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC A Langisi atatsiriza kuthirira mbewu zawo ku dimba, adatsikira kudambo kuti akasambe mmiyendo popeza mudali mutachita matope. +Atangoyamba kusamba, adamva chinthu chawamenya pa mutu ndipo adagwa pansi. +Mosakhalitsa adazindikira kuti adakhapidwa ndi nkhwangwa moti mmene anthu amabwera kudzawathandiza nkuti magazi atachita chosamba. +Nkhaniyo idakatulidwa ku polisi popeza madotolo a pa chipatala chachingono cha Matumba mbomalo adakana kuwathandiza opanda chikalata chochokera ku polisi. +A Kwenda, womwe adavomera kuti ndiwo adavulaza a Langisi adawatsekera. +Pofotokozera apolisi, mlenjeyu adapempha mlimiyo kuti amukhululukire chifukwa adamulasa mwangozi. +Ndidaponya nkhwangwa kuti ndiphe nkhwali koma mwangozi idaphuluza nkukakhapa mayi Langisi omwe sindimadziwa kuti akusamba ku damboko. Chonde ndapota nanu, ndikhululukireni, adatero a Kwenda. +A Langisi ndi mafumu a mderalo adalandira kupepesako ndipo adapempha a polisi kuti amasule a Kwenda. +Koma mafumuwo adalangiza alenje mderalo kuti adzisalama kwambiri posaka kuwopa kuvulaza kapena kupha anthu. +Padakali pano a Langisi akupezako bwino. +Bajeti isautsa Amalawi Patenga nthawi kuti Amalawi adzamwetulire kutsatira ndondomeko ya zachuma yomwe nduna ya zachuma Goodall Gondwe adapereka ku Nyumba ya Malamulo sabata yathayi, malinga ndi akadaulo a zachuma ndi oona mmene zinthu zikuyendera mdziko muno. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Iwo akuti ndondomekoyi ikhala yowawa kwa Amalawi malinga ndi zomwe boma lakhazikitsamo. +Ophunzira pansi pamtengo: Kodi maphunziro angayende? Mwachitsanzo, kuyambira tsopano, boma laika msonkho pa mauthenga a pafoni komanso pa intaneti. Iyi ndi njira imodzi yofuna kuonjezera kutolera ndalama zake za msonkho. +Izi zikutanthauza kuti mitengo yotumizira mauthenga pafoni ngakhale-nso pa intaneti ikweran. Malinga ndi kafukufuku yemwe adachita a Inteernational Telecommunications Union (ITU), mitengo yoimbira foni njokwera nkale mdziko muno kuyerekeza ndi maiko ena padziko lapansi. +Izi zakhumudwitsa mkulu wa bungwe loona ufulu wa anthu ogula la Consumers Association of Malawi (Cama) John Kapito. +Uku ndi kulanga anthu. Aliyense amadalira kulumikizana, ngakhale munthu wa kumudzi amadalira kulankhulana ndi mnzake. Ndiye mpaka kuikapo msonkho? Si ndife okondwa ndi zimenezi, akutero Kapito. +Koma Gondwe akuti izi zili choncho chifukwa dziko lino lilibe ndalama zokwanira kuti Amalawi amve kukoma. +Tilibe ndalama ndipo aliyense akudziwa zimenezi. Zoti ena akudandaula ndi ndondomekoyi si chachilendo ndipo si mbali imodzi yokha yomwe ikudandaula, adatero Gondwe Lachiwiri poyankha mafunso a atolankhani ku Nyumba ya Malamulo mumzinda wa Lilongwe. +Malinga ndi mmene boma lagawira chuma choyendetsera maunduna akuluakulu, unduna wa zamalimidwe chaka chino walandira K133.7 biliyoni poyerekeza ndi K142 biliyoni chaka chatha; unduna wa zamaphunziro walandira K109.8 biliyoni pamene chaka chatha udalandira K127.9 biliyoni; ndipo kuunduna wa zaumoyo kwapita K77.4 biliyoni pomwe chaka chatha zidali K65.2 biliyoni. +Kodi Kapito akutinji ndi mmene zakhalira pamenepa? Bajetiyi ikhala yowawa kwa Amalawi chifukwa maunduna a zaumoyo ndi zamaphunziro, omwe ndi ena mwa maunduna ofunikira kwambiri, sadaganiziridwe. Mwachitsanzo, unduna wa zamaphunziro walandira ndalama zochepa kuyerekeza ndi ndondomeko ya 2014/15. Kodi achepetsa chifukwa chiyani? Ana ambiri akuphunzirabe pansi pa pamtengo; aphunzitsi akusowa nyumba. Ndiye ndi ndalama zochepazi tikwanitsa [kuthana] ndi mavutowa? akudabwa Kapito. +Iye wati unduna wa zaumoyo walandira ndalama zosakwanira zomwe sizingakwanire kukonzera mavuto amene undunawu ukukumana nawo, monga kumanga zipatala komanso kugulira zipangizo mzipatala. +Inde ndalama tilibe, komabe boma likadatenga ndalama ku unduna wa zamalidwe komwe tsogolo silikuoneka. Tikutaya ndalama zambiri chaka ndi chaka ku undunawu kuti tikhale ndi chakudya chokwanira koma njala sikutha; tikumagula chakudya kuti anthu apulumuke ku njala; kodi sangaone pamenepa? akutero Kapito. +Iye wati Amalawi asanamizidwe kuti apeza mpumulo mndondomekoyi koma kuti ayembekezere kulira. Apa palibe kunamizana, mavuto ndiye alipolipo. +Pophera mphongo, katswiri pa za momwe chuma chikuyendera kubungwe la Economics Association of Malawi (Ecama), Henry Kachaje, wati iyi ndi ndondomeko yovuta komanso yowawa chifukwa ikubwera pamene abwenzi akunja adaleka kuthandiza dziko lino. +Uwu ndi muyeso wolemetsa kwa Amalawi pamene talowa chaka chachiwiri popanda thandizo la abwenzi a kumaiko akunja kupatula thandizo lomwe tikulandirabe kuchokera ku African Development Bank (AfDB), akutero Kachaje. +Koma monga akunenera Gondwe, palibe china chomwe boma lingachite pakalipano chifukwa ndalama ndiyo yavuta, kusonyeza kuti Amalawi akonzekere zowawa mchaka chimenechi. +Chaka chatha, ndondomeko ya makuponi ogulira zipangizo za ulimi zotsika mtengo (Fisp) idalandira ndalama zokwana K59.7 biliyoni ndipo anthu 1.5 miliyoni ndiwo adapindula nayo. Chaka chino ndalamayi yatsika kufika pa K40 biliyoni koma anthu amene apindule nayo ndi omwe aja, 1.5 miliyoni. +Funso nkumati kodi zikhala bwanji pamenepa poti ndalamayi yachepetsedwa? Nduna ya zamalimidwe, Allan Chiyembekeza, adati tidikirebe kuti akumane ndi kumvetsa momwe ndondomekoyi ikhalire. +Ndi nkhani yovuta, komabe dikirani tikumane ndipo tinena momwe zinthu zikhalire, adatero Chiyembekeza. +Mavuto ali apo, kumbali yopezera achinyamata mwayi wantchito, zikukhala ngati zisonya. Gondwe adati boma likudalira ndondomeko yopititsa patsogolo ulimi wamthirira yotchedwa Green Belt Initiative (GBI) kuti ndiyo ipereke mwayi wa ntchito kwa anthu ambiri. +Mwachitsanzo, Gondwe akuti boma lili ndi chiyembekezo kuti achinyamata ambiri apeza mwayi wa ntchito ndi polojekiti ya Malawi Mangos ku Salima ndipo anthu 2 000 ndiwo akuyembekezereka kulembedwa ntchito. +Palinso chiyembekezo choti pomafima chaka chamawa anthu oposa 4 000 adzakhala atapeza ntchito kumeneko. +Ku Salima komwekonso kuli polojekiti yopanga shuga pansi pa ndondomeko ya GBl yomwe, malinga ndi Gondwe, ilembe anthu osachepera 5 000, komanso pali chiyembekezo kuti ntchito zina zipezeke ku Karonga, ku Mangochi ndi kunsi kwa chigwa cha Shire. +Nkhani ina yomwe anthu akumidzi angasangalale nayo ndi yakuti pali chiyembekezo choti mtengo wa mabatire oika muwayilesi ndi mutochi mwina atsika mtengo, apo ayi, mwina ukhala chomwecho osakwera chisawawa. +WOPEZEKA NDI MTEMBO MRUMU AKANA MLANDU Henry Juliyo, mkulu wa zaka 29, yemwe akumuganizira kuti adapezeka ndi mtembo wa mwana mchikwama mchipinda kunyumba yogona alendo mboma la Dedza, akuti amutsegulira mlandu wopezeka ndi ziwalo za munthu motsutsana ndi malamulo a dziko lino, apolisi atsimikiza za nkhaniyi. +Mkuluyu, yemwe akuti amachokera mmudzi mwa Nankumba, kwa T/A Kaphuka, mboma la Dedza, akuti amachita bizinesi yogulitsa nyama ya mbuzi zomwe amanka napikula mmidzi, koma pa 4 mwezi uno adadodometsa anthu atamupeza ndi thupi la mwana wakufa mchikwama. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Koma woganiziridwayu akuukanabe mlanduwu kwa mtuwagalu ponena kuti chikwamacho chidali cha munthu wina yemwe adamutenga mwahayala panjinga yamoto yomwe adabwereka kwa mnzake ndipo adagwira chikwamacho ngati chikole kuti munthuyo akatenge ndalama zoti amulipire. +Mneneri wa polisi ku Dedza, Edward Kabango, adati chidatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke mnyanga ndi dandaulo la mnzake, Moses Moya, wa zaka 40, wochokera mmudzi mwa Nambirira, kwa T/A Kachere, mboma lomweli. +Mgwirizano wa awiriwa udali woti Juliyo akabwereka njinga yamoto kwa Moya amauzana tsiku lobweretsa nkupatsana mtengo woti adzapereke pobweza njingayo ndipo zimayenda bwinobwino, adatero Kabango. +Iye adati mwachizolowezi, pa 2 mwezi uno Juliyo adabwereka njingayo kuti akasakire mbuzi mmidzi ndipo adagwirizana kuti abweretsa tsiku lomwelo madzulo, koma mpaka kudacha tsiku linalo. +Kabango adati apa Moya sadadodome kwambiri poganiza kuti mwina mnzakeyo sadayende bwino tsikulo ndipo amayembekezera kuti tsiku lotsatiralo njinga yake ibwera mmawa kapena alandira uthenga koma kudali ziii! Iye adati tsiku litalowa popanda chilichonse, mmawa wa pa 4 Moya adakadandaula za nkhaniyo kupolisi ndipo nthawi yomweyo apolisi adayamba chipikisheni ndipo mwamwayi adatsinidwa khutu kuti munthu wina yemwe ali ndi njinga yamoto akugona kumalo ena ogona alendo paboma la Dedza. +Panthawi imeneyo timayendera zosaka komwe kuli njingayo chifukwa ndilo dandaulo lomwe tidalandira kufikira pomwe anthu ena adatiuza kuti munthu wina yemwe adali ndi njinga yamoto amagona kumalo ogona alendo otchedwa Hideout, adatero Kabango. +Iye adati atafika kumaloko adapezadi njingayo mchipinda chomwe Juliyo amagona koma padali zododometsa chifukwa panjingapo padali chikwama chakuda chachikopa chomwe chimatulutsa fungo loipa. +Mchipinda monse mudali fungo guuu! Apolisi atatsegula chikwamacho adapezamo mtembo wa mwana wazaka za pakati pa 7 ndi 8 ndipo mlandu wina udatsegulidwa wopezeka ndi ziwalo za munthu, zomwe zimatsutsana ndi ndime 16 ya malamulo okhudza za ziwalo za anthu mmalamulo a dziko lino, adatero Kabango. +Panthawiyi akuti khwimbi la anthu lidakhamukira pamalo ogona alendopo kuti adzaone malodzawo pomwe ena amabwera ndi cholinga chokhaulitsa wabizinesiyo poganiza kuti mwina amawagulitsa nyama ya anthu nkumati ndi yambuzi. +Kabango adati apolisi adayesetsa kuteteza wabizinesiyo mpaka kumutengera kupolisi koma akulimbikirabe kunena kuti chikwamacho si chake. +Ngakhale akukana mposamveka chifukwa mtembowo udali mchipinda chake ndipo iye adalimo yekhayekha moti pano tikumusunga kundende ya Dedza komwe akudikirira mlandu wake, adatero Kabango. +Iye adati chifukwa chokanitsitsa kuti sakudziwa kanthu pa za chikwama ndi mtembowo, apolisi akulephera kupeza komwe mtembowo udachokera, koma adati pali zizindikiro zoti mtembowo udachita kufukulidwa. +Thupilo limayamba kuonongeka ndipo limaoneka kuti lidakonzedwa mwachimakolo, zomwe zikusonyeza kuti lidaikidwa mmanda kwina kwake ndipo lidachita kufukulidwa, adatero Kabango. +Akuti pamimba pa mtembowo padali pongamba mkati atavwitikamo zinthu zomwe zimaoneka ngati sanza ndipo adasokapo. +Banki ya mmudzi yadzetsa udani Banki ya mmudzi yadzetsa udani Tili ndi gulu lathu la banki ya mmudzi. Poyamba tidali anthu ochepa koma pano tidachulukana. Timakumana pakhomo la mayi wina ndipo pano adadzipatsa yekha utcheya, ndi mlembi komanso msungichuma. Pano akunena kuti gululi tikamayambiranso tizipereka ndalama yapadera chifukwa amavutika kutilemba mmabuku. Kodi zimatero? BC, Chilumba. +BC, Ayi ndithu zisamatero. Munthu mmodzi maudindo onsewo chifukwa chiyani? Bwanji mukumupatsa mphamvu zonsezo? Nchifukwa chaketu akukutolani mpaka muzilipira ndalama yapamwamba. Muyenera kugwirizana ndi anzanu ena kuti musankhe anthu okhala mmaudindo kuyendetsa gulu lanu. Komanso simuyenera kukumana pakhomo la munthu mmodzi, muzisinthasintha. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Gogo wanga, Banja langa lidatha 2013 ndipo mwamunayo adakwatira, nanenso ndidakwatiwa. Vuto ndi lakuti tikakumana, amandinena kuti ndifera zomwezo ndipo tikakhala limodzi ndi mwamuna wanga amafuna mpaka kuwagunda. Ndichitenji? FC, Zomba. +FC, Apa mpofunika kumulankhula amvetsetse bwino lomwe kuti banja lanu lidatha basi iye alibenso gawo pa moyo wanu. Muyenera kuchita zotheka zonse kuti mumuuze kuti zomwe akuchita zikhoza kukusokonezerani banja. Kupanda kumuuza mvemvemve, apitiriza kuchita khalidwe lake lokolalo. Nzovuta kuti ndikuuzeni kuti musinthe njira chifukwa ndi ufulu wanu kudutsa paliponse komanso nkutheka mukhoza kukumanabe. +Zikomo gogo, Ndakhala paubwenzi ndi mwamuna uyu kwa zaka zitatu. Ndidamuberekera mwana. Vuto lilipo ndi lakuti tikamaseleulana, amakonda kundinena kuti ndine wosaoneka bwino, zomwe zimandikhumudwitsa. Polingalira kuti nthawi zambiri munthu amanena zochokera pansi pamtima. Ndichitenji? MC, Blantyre MC, Zikuoneka kuti izi nzongoseleula chifukwa palibe pamene mwanenapo kuti adakambapo kuti akusiyani chifukwa ndinu wosaoneka bwino. Iyo ikadakhala nkhani ina. Momwe mwafotokozera, izi zimakusautsani choncho ndi bwino kumuuza maso ndi maso kuti izi zimakudetsani kukhosi. Kukambirana ndiko kumatha zonse. +Ndi mwana Gogo, Ndili ndi zaka 24 ndipo zibwenzi zanga zakhala zikumangotha. Koma masiku amenewa mnyamata wina akuonetsa chidwi pa ine. Vuto ndi lakuti iyeyo kwa ine ndi mwana ndiye ndikamuuza, iye amakakamirabe. Ndi chitenji? Mtsikana wanu Msungwana, Chikondi chenicheni si chiona msinkhu. Nkuthekatu kuti mwanayo ali ndi chikondi chimene simungachipeze kulikonse. Ngakhale mutazemba chotani koma ngati Mulungu adakulemberani kuti wanu ndi mwanayo inu mungaletse? Chofunika apa nkuonetsetsa kuti zolinga ndi zofuna zake nzotani. Pali achinyamata ena a ulesi amene masiku ano akufuna amayi okulirapo cholinga adye nawo chuma. Ichi si chikondi. Mumuonetsetse kuti akufuna chiyani kwa inu, musanapange chiganizo.akukhululuka Gogo, Ndili ku Nsanje ndipo ndili ndi chibwenzi ku Blantyre. Anzanga ena amamuimbira foni kumandiipitsira mbiri kuti ndili ndi zibwenzi zambiri. ndikamutumizira uthenga komanso kumuimbira foni sakumayankha ngati kale. Chibwenzi wathetsa ngakhale ndakhala ndikupepesa. Sakukhululuka ngakhale ndikufuna tibwererane. +SL, Nsanje. +SL, Fupa lokakamiza limaswa mphika, akulu akale adatero. Apa zikuonetseratu kuti chidwi mwa inu mwamunayo palibe, chatheratu. Ngati nzoona kuti inu palibe chimene mudalakwa koma a vundula madzi, mtima wanu usavutike chifukwa mudzapeza mwamuna wina. Apa musatayepo nthawi munamukonda mwamuna koma poopa kuswa mphika mutayeni. Iyetu akuoneka kuti ngotengeka ndi za mmaluwa. Adzakupatsani mavuto. +Ofuna mabanja Ndine mkazi wa zaka 34 ndikufuna mwamuna wa zaka 35 kumapita kutsogolo. 0998 501 0901 Ndili ndi zaka 26 ndipo ndimayendetsa minibasi. Ndikufuna mkazi wa zaka za pakati pa 18 ndi 22. 0999 031 842 Ndili ndi zaka 23 ndikufuna mkazi wa zaka za pakati pa 18 ndi 20. Akhale wochokera kumwera. +0995 492 657 Ndine mkhristu wa zaka 26 ndipo sindinakwatirepo. Ndikufuna mkazi woopa Mulungu yemwe ndiwokonzeka kukayezetsa magazi tisanakwatirane. 0994 396 005 Ndili ndi zaka 34 ndipo ndikufuna mayi wa zaka 45 kumapita kumtunda. 01 11 642 230 Ndili ndi zaka 30 ndipo ndikufuna mwamuna wa SDA. Ndili ndi ana awiri. 0884 438 309 Ndikufuna mkazi womanga naye banja. Ndili ndi zaka 25. 0884 538 532 Ndili ndi zaka 31 ndikufuna mkazi wa chibwenzi. 0885 331 478. +Okakamira milongoti zawo izo! Lachitatu likubwelali lidzakhala tsiku lowawa kwa iwo amaonera kanema ya mlongoti (aerial). +Makanema ambiri adzazima ndipo kudzakhala mdima wadzaoneni. Patsikulo ena adzayesa kuzimitsa makanema awo nkuyatsanso koma sadzayaka ndipo ena adzawatengera kwa okonzetsa koma chithunzi osaoneka. Koma awa si mathero a dziko. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Okhawo omwe ali ndi zowayenereza kuonera kanema wawo munjira yatsopano ya dijito adzaona kuwala. Awa ndi mathero a zithunzi zamchengamchenga ndinso zooneka ngati mvula ikuwaza pakanema. +Mchaka cha 2006 bungwe la United Nations (UN) lidagwirizana kuti maiko onse asiye kugwiritsa ntchito zithunzi zamchengamchenga nkupita kudijito. +Bungweli lidati ndi dijito zithunzi za kanema zizioneka zopanda mchengamchega komanso mawu azimveka bwino opanda manzenene. +Koma kodi ndi angati akudziwa za kusinthaku? Mwa anthu khumi omwe tidawapeza mmzinda wa Mzuzu, atatu ndi amene akudziwa za kusinthaku. +A bungwe loona za ogula la Consumers Association of Malawi (Cama) ati boma lilibe nazo ntchito kwenikweni za kusinthaku. +Ndi zoonetseratu kuti boma silikukhudzidwa ndi kusinthaku chifukwa silikudziwa chomwe likuchita, ndi anthu omwe silidawadziwitse mokwanira za kusinthaku, adatero John Kapito, mkulu wa bungweli. +Nayo nduna ya zofalitsa nkhani, Kondwani Nankhumwa, mmbuyomu idavomereza kuti boma lalephera kudziwitsa anthu mokwanira za kusinthaku. +Koma mkulu wa bungwe loyanganira za kusinthaku la Malawi Digital Broadcasting Network Limited (MDBNL), Dennis Chirwa, adati bungwe lake layesetsa kuchita zomwe lingathe. +Iye adati bungwe lake lagula ma decoder omwe akugulitsidwa mmapositi ofesi onse mdziko muno pamtengo wa K20 000. +Amayi akhale odzidalira Mkulu wa bungwe la Beautify Malawi Trust (Beam Trust), Gertrude Mutharika, walimbikitsa amayi mdziko muno kuti akhale odzidalira pachuma. +Mutharika adalankhula izi masiku apitawa pomwe amakhazikitsa tsiku lokumbukira ntchito za mabizinesi la World Entrepreneurship Day mdziko la Amerika.stevggg Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mutharika adati Beam Trust ikufuna kulimbikitsa amayi kutengapo gawo lalikulu pantchito za mabizinesi ngati njira imodzi yowalimbikitsira kudziyimira paokha. +Tayika ndondomeko zingapo zomwe cholinga chake nkupititsira amayi ndi atsikana mmabizinesi. Beam Trust ilimbikitsanso amayi ndi atsikana kutengapo gawo lalikulu pantchito zolimbikitsa ukhondo mmatauni ndi mizinda, adatero iye. +Iye adatsindika kuti kusowa mpamba woyambira bizinesi ndi chikole ndiye mavuto amene amayi ndi asungwana omwe akufuna kuyamba mabizinesi akukumana nawo mu Africa. +Choncho, iwo adapempha mabungwe omwe ndi mabanki kuti aganizire kufewetsa mfundo zawo kuti amayi ndi atsikana adzitha kupeza ngongole mosavuta. +Ena mwa atsogoleri omwe adakhala nawo pamsonkhanowo ndi mkazi wa pulezidenti wa ku Namibia Penehupifo Pohamba ndi mkulu wa bungwe la UN Foundation Cathy Calvin. +Dziwani za matenda a mphere Kutsatira malipoti a kubuka kwa matenda a mphere kuchigwa cha mtsinje wa Shire, uyu ndi tsatanetsatane wa matendawa kuchokera pa zomwe bungwe loona za umoyo padziko lapansi la World Health Organization lidapeza. +Matenda a mphere amakhudza khungu la munthu ndipo amayambika ndi kachilombo kakangono kamene kamapezeka muchakudya. Mchingerezi, Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC kachilomboka kamatchedwa mite ndipo asayansi amakatcha Sarcoptes scabiei. +Kachilomboka sikaoneka chifukwa ndi kakangono kwambiri. Kakalowa pakhungu la munthu, amakanda mosalekeza. +Malinga ndi World Health Organization, matenda a mphere amati ndi okhudzana ndi madzi. Ndi zosadabwitsa kuti lero tikukamba za mphere zomwe zafala kuchigwa cha mtsinje wa Shire komwenso madzi aononga katundu ndi kugwetsa nyumba. +Matendawa amafala ngati kachilomboko kapita pakhungu la munthu wina koma amafala kwambiri pamene munthu amene wakhudzidwa ndi matendawa wakhudzana ndi mnzake monga pogonana mosadziteteza. +Matendawa amafala kwambiri moti mu 2010 anthu oposera 100 miliyoni padziko lapansi ndiwo adakhudzidwa ndi matendawa. +Matendawa mungawadziwe msanga chifukwa pamene akuyamba umangokanda mosalekeza ndipo khungu limatha kusupuka. Zizindikiro zokhala ngati walumidwa ndi udzudzu zimaoneka. +Kukandaku kumafika palekaleka usiku pamene ukugona. Kuyabwakutu kumachitika chifukwa tizilombo tija timakhala tikuyendayenda mthupimo. +Matendawa amafalanso posinthana zovala, zopukutira mukasamba, zofunda. Koma matendawa angathe kukhala pathupi la munthu kwa masiku atatu osapatsira munthu. +Kugwiritsira ntchito mankhwala monga permethrin kapena ivemectin kumachepetsa kufala kwa matendawa koma mpaka lero palibe mankhwala amene amachiza matendawa. +Kukhala munthu wa ukhondo kungathandize kuti usadwale matendawa. Izi ndi zomwe achipatala amalimbikitsa kuti muyenera kumasamba, zovala zizikhala zochapa ndipo malo ogona akhale okonzedwa bwino. +Makanja aphofomoka Makanja, chilombo chomwe chimayenda monyangwa poti chimayangana wina aliyense pamutu kaamba kotalika, chidaona zakuda masiku apitawa chitagwa pamsonkhano wa nduna ya zamalonda. +Pomwe pabwera guleyu anthu amayembekeza kusangalala chifukwa amaoneka modabwitsa komaso amavina modolola mtima. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Izi zidali chomwecho Lachiwiri ku Wovwe mmboma la Karonga, komwe nduna ya zamalonda Joseph Mwanamvekha, kazembe wa dziko la Japan ku Malawi, Shuichiro Nishioka ndi alendo ena olemekezeka adakayendera alimi a mpunga. +Pofuna kuti alendowo asangalale, anthu kumeneko adakonza magule. Ataitanidwa, makanja anabwera pamalo a msonkhano monyangwa. Guleyu adayendera pabwalo modzithemba asanayambe kuvina. +Apa anthu adayembekezera kuti patuluka fumbi koma zachisoni guleyu atangoyamba kuvina adapeperuka ndi kugwa chagada mwendo umodzi utathyoka. +Pofuna kudzichosa manyazi guleyo, adayamba kunamizira kuvina pansi koma anthu otsogolera guleyo adaona kuti zavuta ndipo adapita kukamudzutsa. +Kaamba ka ululu ndi manyazi, guleyo adachoka mbwalo motsimphina ndi kukatsamira galimoto ya nduna kwinaku akumverera ululu. Guleyu adaoneka wosowa mtendere kaamba koti anzake anatenga malo nkuthyola dansi mododometsa kwinaku akufupidwa ndi nduna ndi kazembe wa ku Japan. +Anthu odzigwira adamumvera chisoni makanjayo, koma aphwete adaseka kaamba koti zidali zachilendo kuona makanja akuthyoka mwendo gule ali mkati. +Utatha msonkhano nkhani idali pakamwa idali ya kuphofomoka kwa makanja. Ngakhale Mwanamvekha ndi anthu a ku unduna wake, komaso DC wa boma la Karonga, Rosemary Moyo, sadapirire koma kukambirana za kugwa kwa gule wamtaliyo. +Mwanamvekha adati chidali chinthu chodabwitsa komaso chanchilendo kwa iwowo kuona gule akugwa. +Chifunga pa za boma la fedulo Nkhungu yowirira yakuta tsogolo la boma la fedulo (Federalism) lomwe magulu ena mdziko muno akufuna pamene ena sakugwirizana ndi maganizo otero. +Maganizo a boma la fedulo adabwera chifukwa choti anthu ena akuganiza kuti pali tsankho pa kagawidwe ka maudindo ndi chitukuko mdziko lino. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Jessie Kabwila Mbusa Peter Mulomole, yemwe ndi mneneri wa bungwe la anthu a chipembezo la Public Affairs Committee (PAC) lomwe lidasankhidwa ndi boma kuti limve maganizo a wanthu pa za boma la fedulo, wati anthu akusiyanabe maganizo pankhaniyi chomwe chikusonyeza kuti ambiri sakudziwabe tanthauzo la boma la fedulo. Iye adati ichi ndi chipsinjo ku bungwe la PAC. +Takhala tikugwira ntchito yofufuza maganizo a anthu pa nkhaniyi kuyambira mwezi wa November chaka chatha koma mpaka pano tsogolo lenileni silikuwoneka chifukwa tikulandira maganizo osiyanasiyana, adatero Mulomole. +Iwo adati akumanapo ndi magulu osiyanasiyana mchigawo cha pakati komwe adamva maganizo osiyanasiyana ndipo padakali pano ali mchigawo cha kumpoto komwenso magulu osiyanasiyana akupereka maganizo awo. +Tikukumana ndi mafumu, a mipingo, mabungwe, andale, amabizinesi, ogwira ntchito mboma ndi mmakampani komanso akatswiri mmagawo osiyanasiyana monga zandale, zachuma ndi zamalamulo. Anthu amenewa akutiwuza maganizo awo mosaopa, adatero Mbusa Mulomole. +Mneneriyu adati anthu asayembekezere zotsatira msanga chifukwa nkhaniyi ndiyokhudza dziko lonse choncho nkofunika kuti bungweli litolere maganizo a anthu mofatsa nkupeza chenicheni chomwe akufuna. +Mulomole wakana mphekesera zoti boma ndilo likupereka ndalama zopangitsira misonkhanoyi. +Iwo adati ngati mbali imodzi yokhudzidwa pa nkhaniyi, boma likadapereka ndalama kubungwe la Pac zoti ligwirire ntchitoyi, zotsatira zake sizikadapereka tanthauzo. +Ife ngati bungwe loyima palokha, sitikutenga mbali ili yonse pa nkhaniyi. Ntchito yathu ndiyongofufuza zomwe anthu akufuna; choncho sitikuyenera kulandira ndalama zogwirira ntchitoyi kuchoka ku mbali ili yonse yokhudzidwa, adatero a Mulomole. +Iwo adapitiriza kunena kuti bungwe lawo pamodzi ndi bungwe la chi Katolika lowona za chilungamo la Catholic Commission for Justice and Peace (CCJP) akugwira ntchitoyi ndi thandizo lochokera ku bungwe la United Nations Development Programme (UNDP). +Nkhani ya fedulo idadzetsa mtsutso waukulu kuyambira miyezi ya August ndi September chaka chatha pamene mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika adasankha nduna zake zomwe zambiri zidachokera mchigawo cha kummwera. +Zipani zotsutsa boma ndi magulu ena, makamaka a mchigawo cha kumpoto ndi pakati, adati kuli bwino dzikoli litagawidwa kutengera zigawo ndi cholinga choti chigawo chiri chonse chidzidzipangira chokha ndondomeko za chitukuko. +Phungu wa dera la Hora mboma la Mzimba a Christopher Ngwira komanso wa dera la kuvuma mbomalo a Harry Mkandawire, omwe ndi a chipani cha Peoples Party (PP), ndi ena mwa anthu omwe adayambitsa komanso kulimbikitsa maganizo a boma la fedulo. +Chipani cha Malawi Congress Party (MCP) nachonso chidagwirizana ndi maganizo oyambitsa boma la fedulo. Mneneri wa chipanichi a Jessie Kabwila adati boma la fedulo lidzapangitsa kuti madera onse a dziko liko atukuke. +Kafukufuku yemwe Tamvani adapanga adasonyeza kuti aphungu ambiri aku nyumba ya malamulo sakugwirizana ndi maganizo oterowo kamba koti atha kugawa dziko. +Koma boma lidati anthu apatsidwe mwayi wonena zakukhosi kwawo ngati akufuna boma la fedulo kapena ayi. +Boma silikufuna kupondereza maganizo a wanthu pa nkhani ya boma la fedulo. Aliyense ali ndi ufulu opereka maganizo ake koma izi zichitike poganizira udindo omwe munthu aliyense ali nawo, adatero a Kondwani Nankhumwa, omwe ndi mneneri wa boma. +Pogwirizana ndi a Mulomole, a Nankhumwa adati boma sililowelera pa ntchito yomwe bungwe la PAC likuchita yophunzitsa anthu kapena kufufuza maganizo awo pa za boma la fedulo. +A Nankhumwa adatinso boma silidaperekeo ntchitoyi mmanja mwa bungwe kapena nthambi ili yonse koma lidangotsegula chitseko kwa mabungwe ndi ena omwe angakwanitse kuphunzitsa anthu kuti adziwe ubwino ndi kuyipa kwa boma la fedulo. +Bomatu silidakane kapena kuvomereza boma la fedulo, koma kuti anthu apereke maganizo awo komanso aphunzitsidwe mokwanira. Ichi ndi chifukwa tidalekera mabungwe omwe angakwanitse kuti agwire ntchitoyi ndi ndalama zawo, adatero Nankhumwa. +Koma a Ngwira adati akukaika kuti boma lili ndi chidwi pa nkhani imeneyi. +Tawonapo nkhani zikuluzikulu zikufera mmazira ngakhale komiti yoona nkhanizi itakhazikitsidwa. Kukadakhala kuti boma liri ndi chidwi, likadapereka chithandizo choti anthu omwe akugwira ntchitoyi agwiritse, adatero a Ngwira. +Polankhula ndi Tamvani, katswiri wa zandale ku sukulu ya ukachenjede ya Chancellor College a Blessings Chinsinga adachenjeza kuti nkhani ya boma la fedulo siyofunika kupupuluma. +A Chinsinga adati nkhaniyi ndiyofunika iyende mundondomeko zingapo isadafike pokhazikitsidwa choncho mpofunika kuunika bwino kuti zinthu zidzayenda motani bomalo likadzavomerezedwa. +Choyamba, anthu akufunika kuphunzitsidwa za tanthauzo la boma la fedulo ndi cholinga choti apereke maganizo awo pachinthu chomwe akuchidziwa bwino. Zikatero, ngati anthu avomereza, pakuyenera kukhala voti ya liferendamu. +Pofika popangitsa chisankho cha liferendamu, palinso zofunika kuchita zingapo monga kuunika mmene chuma chizigawidwira, komanso mmene malamulo aziyendera monga kukhala ndi malamulo amodzi dziko lonse kapena chigawo chiri chonse chikhale ndi malamulo ake zomwe sizapafupi, adatero Chinsinga. +Chipako pa nkhani ya simenti, malate Ngati mudakhulupirira lonjezo la chipani cha DPP nthawi ya kampeni chisanachitike chisankho cha pa 20 May 2014 kuti chikadzalowanso mboma chidzatsitsa mitengo ya malata ndi simenti, iwalanipano nyimbo ndi ina, Tamvani watsimikiza. +Mmalo motsitsa malata ndi simenti monga ambiri amayembekezera, boma lati lakonza zomangira nyumba anthu ovutika ndipo ikatha, mwini nyumbayo azidzapereka theka la ndalama zomwe nyumbayo yadya. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mneneri wa unduna wa za malo, Ayam Maeresa, adaulula izi Lachinayi poyankha mafunso a Tamvani itafuna kudziwa za nthawi yomwe anthu ayambire kugula katunduyu motsika mtengo patangotha sabata ziwiri Nyumba ya Malamulo itavomereza K7 biliyoni yothandizira ndondomekoyi. +Tikudikira mvulayi ingotha. Ofuna kukhala pachilinganizochi ayenera kukhala nawo mmagulu amene akhazikitsidwe mmadera awo, adatero Maeresa. +Iye adati pamodzi ndi makhansala undunawo ukha-zikitsa ndi kuphunzitsa magulu oima paokha amene azitchedwa kuti Housing Development Groups. Maguluwa azikhala mwa gulupu aliyense. +Maguluwa ndiwo ayendetse ndondomekoyi ndiponso ndiwo azipeza amene akuyenera kupi-ndula ndi ndondomekoyi. Maguluwo akonzedwa chifukwa munthu aliyense ali ndi makondamakonda a nyumba yomwe akufuna, ndiye ife tizingomanga ndipo tikamaliza mwini nyumbayo azidzalipira theka la ndalama zomwe zagwiritsidwa ntchitozo, adatero Maeresa. +Kusintha kwa ndondomekoyi kukusemphana ndi zomwe anthu akhala akuyembekezera. +Mwachitsanzo, Edison Diverson wa mmudzi mwa Ntaja kwa T/A Dambe mboma la Neno ndipo ali ndi zaka 67, akuti amayembekezera zogula malata ndi simenti zotsika mtengo. Iye wati kusinthaku kwamudabwitsa. +Iye ndi mlimi ndipo adagwira ntchito kumigodi mdziko la South Africa mma 1970. Chibwerereni ku Theba, Diverson sagwira ntchito, mmalo mwake ali pakalapakala kuyendera kuboma kuti amulipire ndalama za ku Thebako. +Khumbo la Diverson mwa zina ndi lakuti ngati angamulipire ndalama zake amange nyumba kumudziko chifukwa akugona mnyumba yofolera ndi udzu ndipo imathonya mvula ikamagwa. +Ndilibe ndalama, sindingakwanitse kugula simenti kapena malata, nzodula kwambiri koma nditamva za ndondomekoyi, ndidali ndi chimwemwe kuti mwayi womanga nyumba uja wapezeka, adatero bambo wa ana asanu ndi awiriyo. +Koma Maeresa akuti kusinthaku kwadza chifukwa cha kukhazikitsidwa kwa pologalamu yomanga nyumba zabwino yomwe akuitcha kuti Decent and Affordable Housing Subsidy Programme (DAHSP) yomwe idakhazikitsidwa ndi mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika ku Msampha 1 kwa T/A Chadza ku Lilongwe mu December chaka chatha. +Iye adati kukhazikitsidwa kwa pologalamuyi kukutanthauza kuti boma liyamba kumangira nyumba anthu ovutikitsitsa mmadera 193 a aphungu onse mdziko muno. +Mneneriyu akuti munthu amene akumangiridwa nyumba azipemphedwa kupeza njerwa, mchenga ndi madzi ndipo ikamangidwa boma lidzawerengetsa ndalama zomwe zalowapo ndipo mwini nyumbayo adzalipira theka la ndalama zomwe zagwiritsidwa ntchito. +Mwini nyumbayi adzakhala akulipira ndalamazo kwa zaka 5. Pali chiyembekezo kuti nyumba pakati pa 80 ndi 100 ndizo zimangidwe mdera lililonse la phungu, adatero Maeresa. +Nthawi ya kampeni chipani cha DPP chidalonjeza zodzatsitsa mtengo wa simenti ndi malata potsutsana ndi njira yomwe chipani cha PP chimachita pomangira nyumba anthu osauka mmidzi. +Nthawi ya kampeni, Peter Mutharika, yemwe pano ndi Pulezidenti wa dziko lino, adati ndi bwino kuti mitengo ya simenti ndi malata itsitsidwe kuti aliyense akhale ndi mwayi womanga yekha nyumba yomwe akufuna. +Atenge ligi yaTNM ndani? Akatswiri pa zamasewero ndiye akamba, aphunzitsi nawo ndi ochemerera alosera zambiri koma kamuna adziwika lero nthawi ikamati 4:00 madzulo ano. +Zonse ndi lero pamene timu ya Big Bullets ndi Moyale Barracks akumane lero pa Kamuzu Stadium masewero amene angadziwitse katswiri wa ligi ya TNM ya chaka chino. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Bullets ili ndi mapointi 56 ndipo yatsala ndi masewero awiri, oyamba ndi a lero ndipo imalizitsa sabata ya mawa ndi Blantyre United yomwe yatuluka mu mligiyi. +Moyale ili ndi mapointi 53, nayonso yatsala ndi magemu awiri, yoyamba ndi ya lero ndipo imalizitsa ndi Blue Eagles yomwe ikuphupha kuti ithere panambala 3 mligiyi. +Ngati Moyale ipambane lero ndiye kuti ligiyi tidikirabe sabata yamawa kuti ithe pamene matimuwa akudzasewera masewero awo womaliza. +Kulepherana mphamvu kwa matimuwa lero kapena ngati Bullets ipambane zipereka chilimbikitso kuti Bullets yatenga ligiyi. +Izi zikusonyeza kuti Moyale ikuyenera kupambana masewero alero ngatidi yathemba zotenga ligiyi. Moyale ikapambana ndiye kuti nkhondo ikhala pa zigoli zochinya ndi zochinyitsa komanso mapointi atatu amene atsala mmasewero asabata ya mawa. +Bullets yachinya zigoli 41 ndipo yachinyitsa zigoli 18. Moyale yachinya zigoli 43 ndipo yachinyitsa zigoli 22. Izi zikutanthauza kuti Moyale ikachinya Bullets ndi chigoli chimodzi komanso kudzachinya Eagles ndi chigoli chimodzi ndiye kuti Bullets ikuyenera kudzachinya Blantyre United ndi zigoli zoposa ziwiri kuti itenge ligi. +Apa nchifukwa ligiyi ili ya masamu zomwe Nicholas Mhango wa Moyale komanso Elijah Kananji wa Bullets akunenetsa kuti ndi bwino kupambana kuti nkhondoyi ichepe. +Masewero andime yoyamba, Bullets idapambana ndi zigoli ziwiri kwa chimodzi ndipo masewerowa adachitikira ku Mzuzu. Lero ndi Kamuzu Stadium yomwe inyamule ntchitoyi. +Anatcheleza: Akundiopseza a gogo wanga Akundiopseza Gogo wanga, Ndili ndi zaka 24 ndipo ndimachokera kwa Kachere mumzinda wa Blantyre koma pano ndili ku Mangochi kumene ndikugwira ntchito mbala ina. +Ndidakwatirana ndi mwamunayo amene ndidamupeza pabala pomwepo patangotha miyezi. Pano tatha chaka ndi miyezi 4 tili pabanja koma tsiku lina mpaka 2 koloko adali akadali kumowa. Nditaimba foni adandilalatira ndipo adandiuza kuti pali akazi ambiri amenenso amamufuna. Ndidanyamula tanga, koma amandiopseza kuti azindimenya tikakumana. +KM, Mangochi KM, Kuopseza ena ndi mlandu. Mosayangana kuti kumbuyoku mumakhala bwanji muyenera kukanena kupolisi. Uwu ndi mlandu ndithu umene ungachititse amuna anu akalewo kuona mavuto. Koma nanu a KM, mwamuna wokwatirana naye mungamupeze kubala? Simudamvepo kuti nkhuku yoweta sagula pamsika? Zofunatu izo! Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Tatalikana Gogo, Ndine mtsikana amene ndili ndi chibwenzi chomwe chimakhala ku Blantyre pomwe ine ndimakhala ku Mzuzu. Takhala chaka chimodzi osaonana koma timalankhulana pafoni tsiku ndi tsiku. Ndikamufunsa kuti ubwera liti kudzandiona amangoti nthawi idzakwana yokha. Kodi ameneyu ali nanedi chidwi? FT, Mzuzu FT, Chikondi sichiona mtunda. Zili bwino kuti mumalankhulana tsiku ndi tsiku. Choncho mukulankhulanako mukhoza kuona ngati chikondi chilipo kapena ayi. Komanso dziwani kuti pamene mukutalikana, nthawi zina chikondi chimazilala. Nkuthekatu apa kuti chikondi cha mwamunayo pa inu chikuzilala. Komanso mbali inayo, bwanji inuyo osayesa kunyamuka kuchoka ku Mzuzu nkudzamuona mwamunayo ku Blantyre? Simunanenepo kuti adakuletsani kuti mukamuyendere ku Blantyre. +Anandilodza Odi agogo, ndinalodzedwa kwawo kwa mwamuna wanga, ndipo ndinapulumuka mwachisomo. Kwathu anati ndibwerere kubanja koma makolo akuchimunawo akuonetsabe kuti sakundifuna. Ndili ndi mantha chifukwa mwamuna wanga alibe nazo vuto. Nditani? BN, Balaka BN, Poyamba simudafotokoze kuti mudadziwa bwanji kuti mudalodzedwa. Ichitu nchifukwa chake boma limanena kuti wotchula mnzake kuti ndi mfiti ayenera kumangidwa. Nkhani zotere zimangodzetsa udani chabe. Ngati mwamunayo akuonetsa kuti akukondani, ndi bwino mubwerere, pajatu banja ndi anthu awiri. +Anatchereza, Ndili pabanja ndi mkazi yemwe akuti ndidamupatsa mimba zaka zisanu zapitazo. Iye adabereka patatha miyezi 8 kuchokera pomwe adandiuza kuti ndamupatsa mimba. Mwanayo sakufanananso ndi ine. Nditani? LC, Mzuzu LC, Palibenso chimene mungachitetu apa kuthetsa banja chifukwa mukukaikira kuti mwana wa zaka 5 si wanu. Nthawi yonseyi munali kuti? Mwadziwa liti kuti mwanayo sakufanana nanu? Pezani chifukwa china chothetsera banja ngatidi mbanjamo muli vuto, osati zimene mukunenazo. +Ofuna mabanja Ndili ndi zaka 20 ndipo ndikufuna mkazi wa zaka zochepera paine. 0996414592 Ndili ndi zaka 26 ndikufuna mkazi wa zaka za pakati pa 20 ndi 24. 0885471466 Ndili ndi zaka 20, ndikufuna mkazi wa zaka 18 mpaka 20. 0888963917 Ndili ndi zaka 30 ndikufuna mkazi wa zaka za pakati pa 35 ndi 40. 0994020379 Zaka ndili nazo ndi 33 ndipo ndikufuna mwamuna. 0998501901. +Mlangizi wa Peter wati akaone zina Ben Phiri, mlangizi komanso wothandizira Pulezidenti Peter Mutharika, Lachiwiri adati watula pansi udindo wake pofuna kupereka mpata woti amufufuze pamanongonongo amene akhala akumveka kuti amachita ziphuphu. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Koma a ku Nyumba za Boma (State Residences) akana kuvomereza kusiya ntchito kwa mkuluyu ati kalata yomwe adalemba youza boma za kusiya ntchitoko ili ndi zina ndi zina zomwe sizikumveka bwino. +Phiri (kumanzere) ndiye ngati akuuza Mutharika: Zikuyenda bwana Tamubwezera kalata yakeyo. Ben Phiri a kontiraki ya zaka zitatu [ndi boma] ndipo ngatidi akutsimikiza kuti afunadi kusiya ntchito, akalembenso kalata yopanda ziyangoyango, adatero mkulu woyanganira Nyumba za Boma, Peter Mukhitho pouza nyuzipepala ya The Daily Times Lachinayi. +Mkalatamo Phiri adati akufuna kusiya ntchito kuyambira pa 1 June, 2105, zomwe ndi zaka 90 kuchokera pano! Ndani adzakhale ali moyo nthawi imeneyo? Mwina a Ben Phiri omwewo, koma ine ndikukaika, adatero Mukhitho. +Koma Phiri adatsimikizira nyuzipepala ya The Nation Lachiwiri kuti iye adatula pansi udindo wake kaamba ka manongonongo omwe anthu ena akumafalitsa kuti iye amaopseza abizinesi, makamaka Amwenye, komanso kuti amasokoneza Mutharika. +Choyamba akuti ineyo ndili ndi ndalama zokwana K800 miliyoni zomwe ndidapeza mnjira za katangale. Ena akuti ndidagula mabasi 20 mosadziwika bwino ndiponso ndili ndi nyumba zambiri ku Area 47 ku Lilongwe, adatero Phiri. +Iye adati kutula pansi kwa udindo wake ndi njira yoti anthu omwe akumuganizira kuti ali ndi milanduwo amufufuze mofatsa popanda kupingika kulikonse. +Mkuluyu adapereka kalata yake yotula pansi udindo atagwira ntchito ndi Mutharika kwa zaka 8 kuchokera pomwe adachoka ku Amereka komwe ankakhala koma adati kutula pansi kwa udindowu si chinthu chapafupi. +Zina zimanyanya. Ndachita dala kuti omwe akufalitsa manongonongnowo andifufuze mokwanira kuti chilungamo chioneke, idatero kalata yomwe adalemba Phiri. +Padakalipano iye akuti akufuna kuika mtima wake wonse pamaphunziro ake ndi kuona kuti mtsogolo muno adzapange chiyani. +Okhudzidwa ndi ngozi ya madzi alandira mbewu Nduna ya zaulimi Dr Allan Chiyembekeza yapempha alimi amene adakhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi kuti abzale mbatata ndi chinangwa chinyezi chisadatheretu mnthaka kuti adzapeze chomwera madzi. +Ndunayo idanena izi masiku apitawa pomwe undunawo umakhazikitsa ndondomeko yopereka mbewuzi kwa alimi amene adakhudzidwa ndi ngoziyo mu January chaka chino. Mwambowo udachitikira mboma la Mulanje. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Maboma onse 15 amene adakhudzidwa ndi ngoziyi ndiwo alandire mbewuyi kuti abzale pamene mvula ikugwabe mmaboma ena. +Ngakhale ndi nkhani yabwino komabe alimi ena akuti izi ndi zosakwanira ndipo boma lisalekere pomwepa. +Olive Chamveka wa mmudzi mwa Mtiza kwa Senor Chief Mabuka mboma la Mulanje adali ndi munda wa maekala awiri koma mundawu udakokoloka. Iye adati mizere 7 yokha ndiyo idapulumuka. +Ndimalima chimanga mmunda umenewu ndipo ndimapha matumba 45. Chaka chino ngakhale thumba la makilogalamu 50 silingakwane. Mavuto awa achimwene, adatero iye. +Chamveka adalandira mbewu ya chinangwa yokwanira kubzala theka la ekala. Ngakhale ena angasangalale ndi mbewuyi, Chamveka sadakondwe. +Mvulatu idasiya kuno, kusonyeza kuti ndidalira chinyontho chomwe chidakalipo zomwe ndi zokaikitsa ngati tingaphule kanthu. Musadabwe kuti sindikusangalala kwambiri. +Boma litipatse chimanga chifukwa tifatu ndi njala. Kupatula zomwe atipatsa lerozi komabe boma lisalekere pomwepa, adatero Chamveka movomerezana ndi Edina Mutakha wa mmudzi mwa Misomali mbomalo amenenso adalandira mbewu ya chinangwa. +Koma Chiyembekeza polankhula atangokhazikitsa ndondomekoyi, adati pali zambiri zomwe boma likuchita kuti likwanitse kuthana ndi mavuto amene anthuwa akukumana nawo. +Iye adati boma lakonza mapologalamu osiyanasiyana kuti afikire alimiwa. +Iyi ndi ndondomeko yoyamba, posakhalitsapa pabwera ndondomeko ya mthirira yomwenso ithandize anthuwa. Izi zichitika pamene alimiwa akudikirira mvula kuti abzale mbewu zina, adatero Chiyembekeza. +Onyanyala ntchito achotsedweMafumu Lukwa (Kumanja) kuwerenga chikalata chopempha Mutharika kuti achitepo kanthu Mafumu mdziko muno apempha mtsogoleri wa dziko lino kuti alowererepo ndi kuchitapo kanthu kwa anthu ogwira ntchito mboma amene akunyanyala ntchito. +Mafumuwa adachita chiwonetsero poyenda mumzinda wa Blantyre Lachiwiri lapitali ndipo adakapereka chikalata cha madandaulo awo kwa mlembi wamkulu wa boma, George Mkondiwa. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mukudandaula kwawo, mafumuwa, omwe adatsogozedwa ndi mafumu akuluakulu mdziko muno, akupempha mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika kuti achotse onse amene akunyanyanyala ntchito ngati sabwerera pantchito. +Mafumuwa adanena mchikalata chawo kuti mdziko muno mavuto a zachuma ndi ankhaninkhani ndipo ndi okhumudwa kuti anthu ogwira ntchito mmakhoti, kusukulu zaukachenjede komanso kubungwe lothana ndi katangale ndi ziphuphu la Anti-Corruption Bureau (ACB) akhala akunyanyala ntchito. +Koma pamene tinkalemba nkhaniyi nkuti ogwira ntchito ku ACB atayamba kugwira ntchito pambuyo pokambirana ndi kugwirizana ndi akuluakulu a boma pa 22 December kuti akonze zina ndi zina. +Mafumuwa, omwe adati akuyankhulira anthu awo kuchokera mzigawo zonse mdziko muno, akuti ogwira ntchitowa akuyenera kumvetsetsa kuti dziko la Malawi lili ndi mavuto a zachuma chifukwa cha kubedwa kwa ndalama mboma komwe kudapangitsa maiko akunja kusiya kupereka chithandizo cha ndalama zoyendetsera chuma cha dziko. +Iwo adati ali ndi umboni woti mndende za mdziko lino muli anthu pafupifupi 300 omwe agwidwa ndipo akusungidwa koposa zaka zisanu popanda kuweruzidwa ndipo kunyanyala ntchitoku kukuonjezera vutoli. +Mfumu yaikulu Lukwa ya ku Kasungu idanena izi powerenga chikalata asadachipereke kwa Mkondiwa: Mafumu pamodzi ndi anthu awo akupempha a Pulezidenti a dziko lino kuti aonetsetse kuti anthu onse ogwira ntchito mboma ayamba kugwira ntchito zawo ndipo aliyense amene akane achotsedwe pompopompo. +Mafumu akupempha anthu ogwira ntchito mboma kukumbukira kuti pakalipano, boma lili kudutsa nyengo yovuta pachuma, ndipo mumiyezi isanu ndi inayi ikubwerayi, mafumu akupempha kuti pasakhale wina aliyense wogwira ntchito mboma kunena zokweza malipiro. +Koma mneneri wa makhoti mdziko muno Mlenga Mvula akuti mafumuwa akunena izi chifukwa chosazindikira chimene ogwira ntchito mmakhoti akunyanyalira ntchito yawo. +Mvula adati mafumuwa awafunse aboma awawuze chimene chikutsitsa dzaye kuti njobvu ithyoke mnyanga kusiyana ndi kumayankhula pankhani yoti sakudziwapo kanthu. +George Nyirenda: Za Flames waiwalako Zambiri zakhala zikulankhulidwa za George Nyirenda amene akusewera mu Caps United mdziko la Zimbabwe kuti atengedwe ku Flames. Iye mwini wakhalanso akufunitsitsa ataitanidwa koma makochi a Flames amangomupatsa nkhongo. BOBBY KABANGO adacheza naye komanso pa za mphekesera yomwe yamveka kuti akubwera kudzasewerera Bullets: Nyirenda: Ndingasewere Bullets basi Moyo uli bwanji ku Caps? Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Zonse tayale madala koma nditangofika kumene ndiye zidatenga nthawi kuti ndizolowere momwe mpira wawo amasewerera. +Kodi udapita liti kumeneko? Mudali mu May chaka chatha. Caps idandipeza pamene ndidali kukampu ya Flames ndipo ndidabwera kuno ngakhale padali kusamvana ndi Bullets, timu yomwe ndimasewerera kumudziko, malinga ndi utsogoleri womwe udalipo panthawiyo. +Tikumva kuti akuchotsa kuti usamasewerenso kumbuyo ndipo wabwera pakati. Chachitika nchiyani? Zoona, panopa tili ndi kochi wina wochokera ku England ndiye wabwera ndi nzeru zake. Ndikusewera bwino moti ndachinya kale zigoli ziwiri. +Osati chifukwa umadzibayanso kumbuyoko? Hahaha! Ayi si choncho, koma adangondikhulupirira kuti ndingachite zakupsa kusiyana ndi ena amene amasewera pakatiwo. +Pali mphekesera ku Malawi kuno kuti ukubwera kudzasewera mtimu yako yakale, kodi izi ndi zoona? Mphekesera chabe, ine ndili kuno kaye ndipo zinthu zikuyendanso bwino. Koma nditakhala kuti ndabwera ku Malawiko ndiyedi palibe timu yomwe ndingasewere koma Bullets basi. Ndidzafa ndikusewerera timuyi, ndi yamagazi. +Wakhala ukulankhulapo za kusiyidwa kwako ku Flames ndipo anthu amati ukuyenera kutengedwa koma sizili choncho. Kodi vuto lili pati? Sindikudziwa kuti vuto nchiyani koma ine ndilibe vuto kusewerera timuyi. Koma dziwani kuti za Flames panopa si mbali yanganso [kwabwino] ndizingopanga za kalabu basi koma za Flames panopa ayi. +Kodi wakhumudwa? Ayi, koma ndangosankha kuti ndizichita za kalabu basi. +Pomaliza, tikumudziwa George kuti ndi rasta wodya zamasamba, kumeneko mwasintha? Kulikonse Rasta ndi Rasta ndipo anandipatsa dzina kuti Jah Love chifukwa cholimba mtima ndi za Chirasta. +Aopa chinyengo pa mayeso a JCE Bungwe lokhudzidwa ndi kayendetsedwe ka maphunziro mdziko muno lati akhumudwa ndi zomwe lidachita bungwe la loyanganira mayeso la Maneb polola ophunzira ena kulemba mayeso a Junior Certificate of Education (JCE) a chaka chino popanda zitupa za umboni (ID). +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe okhudzidwa ndi nkhani za maphunziro la Civil Society Education Coalition (CSEC), Benedicto Kondowe, wati izi zikhoza kuchititsa kuti mayesowa alowe chinyengo. +Polankhula ndi Tamvani Lachinayi lapitali, Kondowe adati ophunzira ambiri adalowa mpakana sabata yachiwiri ya mayesowo, amene adayamba pa 26 May, alibe ma ID ndipo zimadabwitsa kuti oyanganira mayeso amazindikira bwanji ophunzirawo ngati alidi olondola. +Zimenezi, mphunzitsi kapena munthu wina aliyense akhoza kulembera wina mayeso oyanganira osadziwa chifukwa ntchito ya ID nkuthandiza oyanganira mayesowo kuzindikira ngati wolemba mayesoyo alidi iyeyo, adatero Kondowe. +Mkuluyu adati izi zikusemphana kwambiri ndi malamulo oyendetsera mayeso omwe amaletsa wophunzira yemwe alibe nambala kapena ID kulemba nawo mayesowo. +Mneneri wa bungwe loyendetsa mayeso la Maneb, Simeon Maganga, adatsimikiza kuti mayeso a JC adayambadi ophunzira ena alibe zitupa, koma adati mmene limafika tsiku lachinayi akulemba mayesowo ma ID onse adali atapita msukulu zoyenera. +Maganga adati ophunzira pafupifupi 170 000 ndiwo adalemba nawo mayesowa koma adaonjeza kuti nkovuta kunena kuchuluka kwa ophunzira amene adalibe ma ID. +Mmene mayeso amayamba tidali titapereka zitupa msukulu za Kumpoto ndi Kumwera koma tidakhalira ndi sukulu zina mchigawo cha Kumwera chifukwa zipangizo zopangira zitupazo zidali zosakwanira. +Tidayesetsabe moti patatha masiku anayi chiyambireni mayeso tidali titatumiza zitupa zotsalirazo ndipo pano ophunzira onse ali ndi zitupa zawo, adatero Maganga. +Koma Kondowe, yemwe alinso mkomiti yoona kuti mayeso akuyenda bwino komanso kuti palibe zachinyengo, adatsutsa zomwe adanena Magangazo ndipo adati mkati mwa sabata yomwe ino akuyendera mayeso adapeza ophunzira ena akulemba opanda zitupa zikunenedwazo. +Tidapeza ophunzira ena msukulu zina mchigawo cha Pakati ndi ku Shire Highlands akulemba popanda zitupa ndiye zitupazo akapereka liti? adadabwa Kondowe. +Potsutsapo za nkhawa ya chinyengo, Maganga adati a bungwe la Maneb mothandizana ndi oyanganira mayeso komanso akuluakulu a pasukulu amathandizana kuzindikira ophunzira omwe amalowa mchipinda cha mayeso, koma Kondowe adati pagulu lonselo amadziwa anawo bwino ndi akuluakulu a pasukulu moti atafuna kuchita chinyengo akhoza kupusitsa anzawowo. +Takhala tikumva kuti akuluakulu a pasukulu amangidwa kapena kulipitsidwa chifukwa amachita chinyengo pamayeso ndiye angalephere bwanji kupusitsa anzawowo kuti zawo ziyende poti mphunzitsi aliyense amafuna mbiri yake izikoma ana akamakhoza mayeso? adatero Kondowe. +Iye adati bungwe la Maneb likadavomereza kulakwitsa nkusintha kachitidwe ka zinthu kuti mavuto otere asamachitike kawirikawiri. +Kondowe adati pologalamu yokonzekera mayeso a Maneb imasonyezeratu nthawi yomwe ophunzira oyembekezera kulemba mayeso akuyenera kupereka ndalama ya zitupa ndipo akatero bungweri limayenera kupanga zitupazo mayeso asadafike. +Unduna wa zamaphunziro wasamba mmanja pankhaniyi ponena kuti nkhani ya mayeso si ya unduna koma bungwe la Maneb ndipo unduna ntchito yake nkuonetsetsa kuti silabasi ikuyenda bwino. +Nkhani ikadakhala yakuti ana sadamalize silabasi ikadakhala yathu chifukwa ndiyo mbali timayanganira koma nkhani ya mayeso ndi ziphaso mufunse a bungwe la Maneb, adatero mneneri wa undunawu Manfred Ndovi. +Komabe adati sikolondola kulola munthu yemwe alibe ID kulemba mayeso koma ngati unduna akambirana ndi a Maneb kuti zoterezi zisadzachitikenso. +Kondowe adati musukulu 12 zomwe komiti idayendera mchigawo cha Pakati 6 mudapezeka ophunzira omwe amalemba mayeso popanda ziphaso ndipo pulezidenti wa eni sukulu zomwe si zaboma Joseph Patel adapereka lipoti lakuti msukulu 150 ophunzira adayamba kulemba mayeso opanda ziphaso. +Ophunzira amaliza kulemba mayesowo dzulo pa 5 June. +Ulemu kwa Geoffrey Mwale Mkuluyo adali msilikali. Aliyense pa Wenela amamudziwa bwino. Akangoti waledzera, tsikulo ndiye kumakhala ndewu zafumbi. Akapanda kupeza womenyana naye pa Wenela, zonse zimakathera kwa mkazi wake. +Tonse tikudziwa kuti samasiya ndalama za ndiwo pakhomo msirikaliyo. Mkazi amati akafunsa ndalama ya pakhomo, makofi. Akati anawa chakudya, kukunthidwa ngakhale ndi zitsulo. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ukhoza kukachita ngakhale uhule upeze yodyetsa anawa, adali kutero msirikaliyo. +Koma akangomva kuti mwamuna wina kumsika wamupatsa mkaziyo bonya waulere, nayenso ali pamoto. +Adali wozunguza. +Ngakhale kupita kutchalitchi adaleka kalekale. Ena ankamutcha Boko, ena akuti Isisi. Koma adali msirikali basi. +Tsiku lina adautunga kuyambira mmawa mpaka usiku. Amachoka kumowako nthawi itangodutsa 10 koloko. Wapamalopo atafunsa kuti amulipire, adalandira zibakera. +Atafika kunyumba, adapeza kalata ili pakhonde. +Chigawenga msirikali woipitsa dzina la asirikali anzako, munthu wa nkhanza kuposa Satana. Wandizunza mokwanira, ndamanga ulendo wakwathu. Komabe ndakusiyira chakudya chimene anzako anagula. Ndatengedwa ndi anzakowo, munthu wopanda nzeru iwe. Kukhakhala mtima ngati wakwananda kapena msana wa fulu. Estere. +Estere adali mkazi wa msirikaliyo. Adalowa mnyumba. Adafikira patebulo pomwe padali mbale ziwiri zovindikira. Adadziwiratu kuti mwinamo mudali nsima, mwinamo ndiwo. Kukhosi kudachita kuti dyokodyoko. Dovu lidati liyambe kuchucha. +Adayamba wasamba mmanja. Nthawi yopemphera adalibe. Mtima udali kugunda. Adavundukula mbale yoyamba, mudali miyala itatu. Miyala, osati mitanda itatu! Adatsegula mbale yachiwiri. Mudali masamba awiri a gwafa osaphika nkomwe. Adali atathiridwa tomato ndi mchere. +Msirikali adakwiya. Adayatsa fodya wamkulu amene ankasunga mujombo. Adayamba kukoka. Utsi sumatuluka nkomwe, amaupanirira. Amachita ngati akubanika. +Atatha kusutako, adakhala pansi. Momwe adagonera sadadziwe! Adayamba kulota. +Adalota kuti adali atamwalira. Adafika kumwamba, pampando wachifumu. Woweruza anthu abwino ndi oipa adamuuza mkuluyo kuti adamupatsa mwayi wolapa koma iye sadafune kulapa. Adamupulumutsa kungozi komanso matenda koma sadafune kulapa. Udali kukonda ndewu, kumenya mkazi ndi ana ako. Tsono ndikupatsa mwayi umodzi wobwerera kudziko lapansi. Subwerera ngati munthu. Sankha chinyama chimene ukufuna, adatero woweruzayo. +Msirikali uja adayamba kudya mutu: Ndisanduke mkango? Ndikaphaphalitsa nyama zina zakutchire. Koma ayi, alenje akandipha chifukwa akufuna chikopa, mchira ndi matumbo anga. Ndisanduke njovu, nyama ndi anthu azikandiopa. Koma ayinso, mnyanga wanga ukandiphetsa! Nanjinanji kusanduka nyani ndiye sindikalimba. Akandipha kuopa kuwapatsira ebola. +Pamapeto pake, adasankha kukhala kangaude. Choncho nditsetsereka kudziko nkukakhala mnyumba yogumuka zakazaka. Womulenga adamuuza: Chabwino, usanduka kangaude. Bwerera kudziko lapansi. +Apa mpomwe mkulu uja adadziwa kuti tsopano azitulutsa ulusi muja achitira kangaude. Hmmmmm! Hmmmmm! adali kutero, uku akumva kuti ulusi ukutuluka ndipo iye akutsikira kudziko lapansi. +Hmmmm! Hmmmmm! adapitiriza, ulusi ukutuluka. Posakhalitsa adayamba kuona dziko lapansi. +Hmmmm! Hmmmmm! adatsikirabe, ulusi ukutuluka. Kenako adafika padziko lapansi. +Adayangana kumwamba ndipo dzuwa lidamuthobwa mmaso. Apa mpamene msirikaliyo adadzidzimuka kutulo kwakeko. Poti atembenuke, adazindikira kuti wadzionongera. +Abale anzanga, mwinatu sindidakuuzeni, msirikaliyo ndi mmodzi mwa asirikali amene adamenya mnyamata wina timu yawo itagonja pampira wa dolola umene udalipo pa Wenela. Mnyamatayo adatisiya momvetsa chisoni, ndipo pano msirikaliyo limodzi ndi anzakewo sakudziwika kumene ali. +Umphawi ukukolezera mchitidwe wogwiririra Pamene mabungwe ogwira ntchito mmidzi ku Ntchisi ali kalikiriki kudziwitsa anthu za kuipa kwa nkhanza zochitira ana ndi amayi, zikuoneka kuti mchitidwewu ukunka nupita patsogolo chifukwa cha zikhulupiriro zina mbomali zimene zimachititsa abambo ena kugwiririra amayi ndi ana pofuna kulemera. +Mmodzi wa akuluakulu a bungwe lounika za ufulu wa ana ndi amayi komanso nkhanza kwa amayi lotchedwa Ntchisi Womens Forum mbomali, Febby Kabango, adauza Tamvani Lachiwiri kuti bungwe lawo ndi lokhudzidwa kwambiri ndi kuchuluka kwa nkhani zogwiririra ana ndipo wati izi zikuononga chithunzithunzi cha nkhondo yolimbana ndi kuthetsa nkhanza komanso ufulu wa ana ndi amayi. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Umphawi ukukolezera mchitidwe wogwiririra Chiwerengero cha milandu ya nkhani zogwiririra mboma la Ntchisi chikuonetsa kuti milanduyi idakwera papolisi ya paboma ndi 10% chaka chatha chifukwa polisiyi idalandira nkhani zokwana 27 zogwiririra kusiyana ndi milandu 25 yomwe idalandiridwa mchaka cha 2013. +Malingana ndi Kabango, nkhani zogwiririra zikuchuluka kwambiri mbomali kaamba ka zikhulupiriro za anthu ena zofuna kulemera mwamsanga akauzidwa ndi asinganga kuti akagonane ndi ana awo ngati akufuna kulemera. +Iye adati kafukufuku yemwe akhala akupanga mbomalo kwa ma T/A asanu ndi awiri kwa Kalumo, Nthondo, Kasakula, Malenga, Chilooko, Vusojere ndi Chikho, adasonyeza kuti nkhani zogwiririra mbomali zikuchuluka chifukwa cha zikhulupiriro zofuna kulemera. Adapereka chitsanzo chakuti ngati wina walima fodya wambiri amatha kupita kwa singanga kuti ngati akufuna kuti malonda ake akayende bwino kumsika, ayenera kukagonana ndi mwana, mchemwali kapenanso mayi ake, zomwe ndi zikhulupiriro zachabe. +Abambo ena amene amasunga ana owapeza amagwiriranso anawa ndi kuwatenga ngati akazi awo, zomwe ndi mchitidwe woipa komanso kuphwanya ufulu wa anawa, adatero Kabango. +Tikugwira ntchito ndi apolisi, a khoti, a jenda, a zaumoyo ndi unduna wa achinyamata kuti mchitidwe wogwiririra ana uchepe kapena utheretu, adaonjezera Kabango. +Mkulu wofufuza papolisi ya Ntchisi, Sub-Inspector Frazer Kamboyi adati kafukufuku wa apolisi akusonyeza kuti nkhani zogwiririra zakhala zikuchuluka mbomali chifukwa cha zikhulupiriro za anthu ena kuti akagona ndi mwana wamngono alemera ngati alima fodya; ngati ali ndi matenda a mgonagona akagonana ndi mwana achira; komanso ena kumangokhala kusowa umunthu. +Anthu awiri mbomali adamangidwapo pankhani zogwiririra ana atanamizidwa ndi asinganga kuti ngati afuna alemere akagone ndi ana awo kapena ena mwa abale awo, adatero iye. +Adapereka chitsanzo cha Amoni Dzoole wa zaka 26 wochokera mmudzi mwa Mbewa, T/A Chilooko mbomalo, yemwe adamangidwa zaka 10 kaamba kogwiririra mwana wa zaka 12 wa mchimwene wake pofuna kukhwimira bizinesi yake yogulitsa nyama ya nkhumba ndi tchipisi komanso kuteteza ndalama zake kuchitaka. +Winanso, Mateyu Kaputa, wa zaka 21, wa mmudzi mwa Nandeta, mdera la T/A Vusojere mbomali, adamangidwanso zaka 10 kaamba koti adapezeka wolakwa pamlandu wogwiririra mwana wake wa chaka chimodzi ndi sabata zitatu pofuna kukhwimira malonda ake a fodya kuti akayende bwino kumsika. +Mkulu wina wa mmudzi mwa Mfumbati dera la T/A Nthondo mbomali, yemwe adati tisamutchule dzina, adati adapita kwa singanga kuti malonda ake a fodya amuyendere bwino ndipo adauzidwa ndi ngangayo kuti akagonane ndi mwana wa mchemwali wake zomwe adakana. +Komanso mkulu wina mmudzi mwa Gamba, T/A Chilooko mbomali adapita kwa singanga kuti akhwimire bizinesi yake ya golosale ndipo adauzidwanso kuti akagonane ndi mwana wake. +Mmodzi mwa a singanga ku Ntchisi, Kafani Kapadyapa, wa mmudzi mwa Chikhutu, dera la T/A Kasakula mbomali, yemwe wakhala akuchita usinganga kuyambira mu 1975, adati nzoona pali asinganga ena amene amanamiza anthu kuti ngati akufuna kulemera akagonane ndi mwana kapena mbale wake. +Singangayu adati ngati pali asinganga amakhalidwe oterewa asiye kumanamiza anthu chifukwa akuononga mbiri yabwino ya dziko la Malawi ndipo adati uku kumangofuna kunyenga anthu osati kuwathandiza komanso kuwabera ndalama. +Polankhulapo pa nkhaniyi, mfumu T/A Malenga ya mboma la Ntchisi yati iyo ndi yokhudzidwa kwambiri ndi kuchuluka kwa nkhani zogwiririra mbomali. +Kupatula kwa kusowa chikhalidwe, kukhala ndi zikhulupiriro zofuna kulemera mwansanga akagwiririra ana ndi achibale kwa makolo ena komanso kusuta fodya ndi kumwa mowa kwa achinyamata ndi zifukwa zikuluzikulu zomwe zikupangitsa kuti nkhani zogwiririra zichuluke mboma lino la Ntchisi, adatero Malenga. +Mfumuyi yapempha mabwalo a milandu kuti adzipereka zilango zokhwima kwa amene apezeka olakwa pankhanizi komanso apempha apolisi kuti azifufuza nkhanizi mofulumira ndi cholinga choti tsogolo la nkhanizi lizidziwika kotero kuti mchitidwewu utheretu. +Koma T/A Kalumo wa mboma lomweli, pamene akugwirizana ndi zimwe wanena Malenga, wati kusavalanso bwino kwa atsikana ndi amayi ena kukupangitsanso kuti mchitidwe wogwiririrawu uchuluke. +Tidalephera kuyankhula mneneri wa kulikulu la apolisi kuti atipatse chithunzithunzi cha kukula kwa mchitidweu mdziko muno. +Asanu anjatidwa atakana kupeleka magazi Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Govt to review Genset deal Abambo asanu a mboma la Mangochi anjatidwa powaganizira kuti adalephera kupereka magazi kwa mwana wa zaka 7 kaamba ka zikhulupiriro za mpingo wawo. +Malinga ndi mneneri wapolisi ya Mangochi, Rodrick Maida, abambowa adatengera mwana kuchipatala cha Koche Health Centre komwe adakamugoneka akudwala malungo. +Koma anamwino atamupima akuti adaona kuti mwanayo ankasowa magazi kotero adapempha mmodzi mwa abambowo amene ndi bambo ake kuti apereke magazi. +Akufuna kwabwino ngati anthu awa akupulumutsa miyoyo. +Bamboyo Saimoni Kamwendo wa zaka 44 ndipo yemwe amachokera mmudzi mwa Mapata kwa T/A Mponda ku Mangochi komweko, adakana kuti sangapereke magaziwo. +Maida adati bamboyo atakana, anamwinowo adapempha amalume a mwanayo omwe adalipo atatu kuchipatalako kuti apereke magazi koma nawonso adakana. +Achipatalawo adapempha agogo a mwanayu, Bernard Kamwendo, kuti apereke magaziwo koma nawonso adakana kupereka magaziwo ponena kuti ndi ampingo wa Mboni za Yehova ndipo samaloledwa kupereka magazi, adatero Maida. +Iye adati nthawiyo mwanayo amasowa magazi kuti akhale moyo ndipo adamutengera kuchipatala chachikulu cha Mangochi pamene sisitere yemwe amayanganira chipatala cha Koche, Elizabeth Kamuikeni, adati apereka magaziwo. +Kamuikeni adapereka magaziwo ndipo mwanayo adayamba kupeza bwino mpaka amutulutsa mchipatala. +Ngakhale iyi idali nkhani yabwino koma kwa amunawa idali yowawa chifukwa kulandira kapena kupereka mankhwala kwa wodwala si ziloledwa ndi zikhulupiriro za mpingo wawo. +Amunawa adayamba kuopseza kuti amutengera kubwalo la milandu sisitereyo popereka magaziwo. Achipatala adatidziwitsa tidathamanga ndi kudzamanga amunawa. Tawatsegulira mlandu wolephera kupereka thandizo kwa mwana zomwe zikusemphana ndi gawo 242 la malamulo ndi zilango zake ndipo chilango chake ndi zaka zitatu mndende ukugwira ntchito ya kalavula gaga, adatero Maida. +Koma mmodzi mwa amene amapemphera chipembedzochi ndipo sadafune kutchulidwa dzina adati ndi zoona kuti kulandira kapena kupereka magazi sikololedwa ndi chikhulupiriro chawo. +Iye adati izi samangochita koma pali malembo a mbaibulo amene amatsimikizira mfundoyi. Iye adatsindika kuti ndi bwino kuchita mosangalatsa Mulungu kulekana ndi kusangalatsa munthu. +Komabe mpingowu uli ndi nthambi yomwe imafotokozera bwino nkhani zotere. Ndikhulupirira kanthawi kena mudzacheza nawo kuti adzatambasule bwino chomwe malembo amanena pa nkhaniyi, adatero. +Nkhani ya amunawa idalowa mbwalo la milandu pa 24 April ndipo ikuyembekezerekanso kulowanso pa 27 May pamene mbali ya boma ibweretse mboni zina ziwiri omwe ndi ogwira ntchito pachipatala cha Koche. +Amalume a mwanayu ndi Solomon Mwabwino wa zaka 29, Diverson Wabwino wa zaka 21 komanso Baison Chindanda wa zaka 40. +ANATCHEZERA Adatidyera ndalama Zikomo gogo, Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Timakumana banki ya mmudzi pakhomo la mayi wina yemwenso adakakamira kuti azisunga ndalamazo. Iye adatenga ndalamazo ndi kuchitira chinkhoswe. Litakwana tsiku logawana adati amukawa achitaka ndipo adati tisonkhe. Titasonkha adati sizidakwane, tikuyenera kusonkhanso ndalama zina chifukwa imaperewera K170 000. Titani? BCA, Karonga. +BCA, Kaneneni kupolisi basi. Uku nkuba mopusitsa. Palibenso china chimene mungachite. Ndipo mudalakwa kusonkhanso ndalamazo. +Amagwiranagwirana Zikomo gogo, Ndili pachibwenzi ndi mkazi wina amene amakhala ku Blantyre pomwe ine ndili ku Balaka. Nthawi zina bwenzi langalo amapita kwa mnzanga komwe amagwiranagwirana. Zikatero mnzangayo amandiuza zonse zinachitika. Kodi mnzangayo akundikonda? BK, Balaka. +BK, Funso lisakhale lakuti kodi mnzanuyo akukukondani, koma kuti kodi mkazi wanuyo akukukondani? Ayi ndithu, ndipo mukadakhala ena mukadangomusiya. Mukhoza kutuma anthu ena afufuze ngati mnzanuyo amachita izi ndi bwenzi lanulo. Chifukwatu akhoza kukhala kuti akungofuna kuti musiyane. Apatu mukamati amagwiranagwirana mukutanthauzanji? Zingatheke izo? Ndikuonatu ngati amenewo amapitirira mpaka kuchita zachiwerewere. Samalani, phukusi la moyo sakusungira ndi mnzako. +Ndikufuna ana anga Ndili ndi zaka 20 ndipo banja ndi mkazi wanga lidatha tili ndi ana awiri. Anawo ali kwa agogo akuchikazi koma ndikati ndikawatenge amandikaniza. Komanso kodi banja likatha ana apita kumpingo wa mayi awo kapena bambo awo? SF, Dowa. +SF, Nchifukwa chake ambiri amalimbikitsa kuti ndi bwino kukwatira munthu wolingana naye zikhulupiriro: ana sachita kusankha kuti apite mpingo wa bambo kapena mayi awo. Nanga inu banja lanu mudamangitsa bwanji? Pomwe limatha mgwirizano udali woti ana apite kuti? Nanga chisamaliro cha kholo linalo chizikhala motani? Dziwani kuti ngakhale banja lithe, makolo a anawo ndi omwewo basi, choncho ndi ufulu wanu kuwasamalira mwanjira iliyonse. Kaneneni nkhaniyi kwa ankhoswe anu ngakhalenso kupolisi yoyanganira za mbanja. +Tibwererane? Anatchereza, Ndidali ndi chibwenzi pamene ndinkakhala ku Mzuzu. Koma nditasamukira ku Lilongwe ndidamva kuti amayenda ndi mphunzitsi wina. Nditamufunsa amayankha zosalongosoka ndipo adathetsa chibwenzi. Koma pano akuimba foni ati ndimukhululukire. Tsono nditani poti ndidapeza wina? R, Lilongwe. +R, Ndimanena kawirikawiri kuti kukhala kutali nthawi zina kumachititsa chikondi kuzilala. Poti mwati mudapeza wina, pitirizani ndi ameneyo chifukwa simukudziwa chifukwa chimene akufuna kuti mubwererane. Nkutheka kuti pano ndi mphunzitsiyo zasokonekera. Mtsogolo mwabwino, kumbuyonso kwabwino. +Ndamuonongera zambiri Zikomo gogo, Ndidakhala pachibwenzi ndi mkazi wina kuyambira 2010 mpaka 2013. Adathetsa chibwenzi mu 2014 pomwe ankandinamizira kuti ndili ndi mkazi wina. Pano amandiimbira kupempha zosiyanasiyana ndipo ndimamugulira koma ndikamuuza kuti tikumane amati watangwanika. Nditani, ndamuonongera zambiri. +JS, Lumbadzi. +JS, Pomugulira zinthuzo mumati mukutani? Apatu sindingakuikireni kumbuyo chifukwa mukudziwa chimene mukuchita. Ndingonena kuti onani momwe ndayankhira R pamwambapa. +Othawa madzi ati bola azibwerera kwao Mawu oti kwanu nkwanu mthengo mudalaka njoka lero akupherezeka pomwe anthu ena amene adathawa madzi osefukira kumunsi kwa chigwa cha Shire, maka ku Nsanje, akuti akufuna boma liwalole azibwerera kwawo ponena kuti ndi bwino akavutike kusowa pogona koma azikalima. +Nyakwawa Katandika ya kwa T/A Nyachikadza yomwe ikusungidwa pamsasa wa Bitilinyu mbomalo, yati iyo ndi anthu ake akuopa kuti ngati sabwerera msanga ndiye kuti sakhala ndi mwayi wolima, zomwe zingawabweretsere njala yoopsa chaka chino mpaka chamawa. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Anzathu chimanga chikupota, pamene ife sitidayambe ndi kulima komwe. Mvula sichedwa kusiya kuno. Ngati tingokhala mmisasamu, ndiye kuti tikuputa dala njala, Katandika adauzaTamvaniLachiwiri. +Koma mkulu woona zomangamanga kuofesi ya DC wa Nsanje, Kennedy Adamson, wanenetsa kuti ngati anthuwo akufuna kupita kapena akukakamirabe mmalo angoziwa ndiye sapeza nawo mwayi wa nyumba zotsika mtengo. +Boma limanga nyumba zotsika mtengo mmadera amene simukhudzidwa ndi ngozizi. Ndiye ngati ena akukana kusamukira kumtunda kapena akubwerera [mmalo momwe chaka ndi chaka mukhala vuto la kusefukira kwa madzi], sapindula nawo ndi ndondomekoyi, adatero Adamson. +Koma Humphrey Magalasi, amene akuyanganira msasa wa Bitilinyu, akuti ngakhale anthuwa akukakamira kubwerera, pali mantha kuti angakavutike chifukwa madzi sadaphwerebe. +Kodi akuti apita kuti? Kuli madzi okhaokhatu komwe amakhalako. Ngati panopa tidakasakabe kuti tipeze anthu amene tikuwaganizira kuti adapita ndi ndipo sadapezekebe, ndiye kuti zinthu zili bwino kumeneko?, adatero Magalasi. +Nawo azanyengo achenjeza kuti kugwa mvula yoopsa kuyambira Lachinayi lathali ndipo pali chiyembekezo kuti ku Chikwawa ndi ku Nsanje madzi asefukiranso. +Mneneri wa nthambi yoona zanyengo Elina Kululanga wati maboma a Blantyre, Zomba ndi Mulanje ndiwo ali pachiopsezo cholandira mvula yochuluka. +Ikhala yaziphaliwali komanso yamphepo ya mkuntho. Ndi mvula yambiri, chiyembekezo chilipo kuti kuchigwa cha Shire madzi asefukiranso, adatero Kululanga ouza Tamvani Lachiwiri. +Kodi nyakwawa Katandika akuti chiyani pa zomwe odziwa zanyengo akunenazi? Iyo ikufotokoza: Chadutsa chija ndi chinyama, sizingatheke kuti madzi otere adutsenso. Ineyo chibadwireni sikunadutseko madzi ngati amenewa. Tisaope, madzi amene aja apita. Malo olima alipo, tikalima kumtunda chifukwatu madziwa aphwerako kusiyana ndi momwe timachokako. +Kwa maola awiri amene Tamvani idakhala pamsasa wa Bitilinyu womwe ukusunga anthu oposa 3 000, nkhani yomwe anthu ambiri amakamba ndi yoti abwerere kwawo basi. +Ngakhale zakudya zikubwera pamsasawu, anthuwa akuti sakukondwa ndi momwe akuwagawira chakudyacho. +Tikuyenera tizidya katatu patsiku, koma tikumadya kawiri basi, komanso chakudya chake chochepa. Kodi ngati sitilima ndiye tizivutikabe chonchi? Boma litipatse mapepala apulasitiki kuti tikamangire nyumba ndipo litivomereze kubwerera kwathu, idatero mfumuyi yomwe idatinso mudzi wake wonse udathawa madzi oopsawo. +Izinso zili chonchi ndi kumsasa wa Makhanga ndi ku Osiyana mbomalo komwe, malinga ndi mkulu wa zaulimi Isaac Ali, anthu ena ayamba kale kutuluka mmisasa yawo. +Ndauzidwa kuti anthu ena akwezedwa mabwato ndipo abwerera. Akuti akukhala cha ku Khonjeni mbali ya Thyolo komwe kulibe chakudya. Kupitako nkovuta chifukwa cha mayendedwe, adatero Ali. +Mvula ya mphamvu idagwa kumayambiriro a mwezi uno ndipo maboma a Chikwawa, Nsanje, Phalombe, Zomba, Rumphi, Karonga, Thyolo, Machinga, Mangochi, Ntcheu, Chiradzulu, Mulanje, Balaka, Salima ndi Blantyre ndiwo adakhudzidwa. +Malinga ndi zomwe mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika walankhula Lachiwiri lapitali, anthu 174 000 atsamutsidwa mmalo mwawo kaamba koti nyumba zawo zakokoloka ndi madzi. +Iye adati sukulu 234 zagwetsedwa ndipo sukulu 181 ndizo zikugwiritsidwa ntchito ngati malo othawirako. +Mutharika adati chiyambireni mavutowa, boma lake lakhala kalikiriki kuthandiza anthu amene akhudzidwawa ndipo ndalama zoposa K38 biliyoni ndizo zikufunika kuti zithangate anthuwa. +Mgodi wa Kanyika waika anthu pamoto Anthu okhala ku Kanyika mboma la Mzimba ali pachiopsezo chachikulu cha umphawi komanso njala ataletsedwa ndi boma komanso kampani ya Globe Metals and Mining kupanga chitukuko komaso kulima kuderali zaka zitatu zapitazo pofuna kupereka mpata woti kampaniyi iyambe kukumba miyala ya mtengo wapatali kumeneko. +Mabanja 248 ndiwo akukhudzidwa ndi nkhaniyi ndipo sadapatsidwebe chipukuta misozi kapena malo ena oti azikakhalako ngakhale kuti iwo adalonjezedwa kuti apatsidwa ndalama ndi malowo. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Izi zadzetsa mavuto kuderali kaamba koti nyumba zidayamba kugwa chifukwa choti sizikusamalidwa chifukwa padali chiyembekezo choti iwo achoka. Nyumba 45 zidagweratu moti anthu akukhala muzisakasa, makhitchini, zotsalira za nyumba komanso ena adapita kwa achibale. +Bungwe la Chikatolika loona za maufulu a anthu la Catholic Commission for Justice and Peace (CCJP) masiku apitawa lidakonza ulendo wa atolankhani kuti akadzionere okha mavuto omwe anthu agwamo. +Mavuto omwe anthu akukumana nawo, komanso chetechete wa boma ndi kampaniyi, zapangitsa mafumu ndi anthu a kuderali kuti ngati sachitapo kanthu pa za chipukuta misozi pofika pa 31 March, apanga zoti kampaniyi ichoke basi. +Mavutowa afikaso popsesa mtima Inkosi ya Makhosi Mmbelwa yemwe akuti ngati kampaniyi ndi boma sali okonzeka kuyamba ntchito ya mgodi ndi bwino kuti awasiye anthu azikhala mmene akhalira mmbuyomo. Mkulu woyongana za miyala ndi nthaka wa ku Globe Metals and Mining, Chris Ngwena, adati kampani yawo singalankhulepo pankhaniyi kaamba koti pali zokambirana ndi boma. +Koma mlembi wamkulu kuunduna wa zachilengwe ndi migodi, Ben Botolo, adati anthu adekhe chifuKwa kampani ya Globe ikuyangana makampani ena oti ithe kugwira nawo ntchito. +Asemphana maganizo pa zoletsa masacheti Pali kusemphana maganizo kutsatira kulengeza kwa boma kuti laletsa mowa wa mmasacheti umene Amalawi ena akhala akuthudzulira. +Pamene mafumu ena akugwirizana ndi ganizoli, ena akuti palakwika ndipo boma libweze moto. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Msonkhano wa nduna pa 16 February udavomereza zoletsa mowawu. +Kuletsaku kumatsatira chigamulo cha bwalo la milandu lomwe lidati nthambi yoona kuti katundu wopangidwa mdziko muno akukhala wa pamwamba la Malawi Bureau of Standards siyilidalakwe kuletsa makampani wotcheza mowawo kuleka kutero. +Nkhaniyi pano yabwerera kukhoti pamene makampani amene amafulula mowawu atengera nkhaniyi kubwalo lalikulu kusaka chigamulo china. +Kulengeza kwa bomaku kudadzetsa mpungwepungweena akudana ndi lingaliroli, pomwe ena akugwirizana nalo. +Mwachitsanzo, msabatayi mkulu amene wakhala akumenya nkhondo yoletsa mowawu, Jefferson Milanzi, wa bungwe la Young Achievers for Development (YAD), adafuna kupandidwa ndi anyamata ena ku Zingwangwa mumzinda wa Blantyre polimbikira kuti mowawu uletsedweretu. +Adalipo anthu pafupifupi 15 omwe amati ndinene chifukwa chimene mowawu wandilakwira. Adati athana nane chifukwa cholimbikitsa nkhondo yoletsa mowawu, adatero Milanzi amene akuti adathamangira kupolisi ya Soche mumzindawu kukadandaula. +Nawonso mafumu ena adauza Tamvani msabatayi kuti palakwika kuletsa mowawu chifukwa achinyamata amapezerapo phindu pogulitsa mowawu. +Senior Chief Nthache mboma la Mwanza akuti achinyamata ambiri mmidzimu akhala akupha makwacha ochuluka pogulitsa mowa wa mmasachetiwu. +[Zoletsa mowa wa mmasachetizi] ndiye ziwonjezera umphawi wathu wakalewu. Ndiye achinyamata azitani? Ngatitu kuli bizinesi yomwe imawapatsa ndalama zochuluka achinyamata kumudzi kuno ndiye ndi mowawu, adatero Nthache pouza Tamvani. +Nthache adati si mowa wokha wa mmasacheti umasokoneza achinyamata kotero sakuona chifukwa choletsera. +Kuli mowa wa kachasu womwenso ndi mowa woipa kwambiri. Kuli mtonjani komanso ena amasuta chamba. Ndiye si masacheti okha amene ali ndi vuto. Boma liganizepo bwino pamenepa, adatero Nthache, amene adati samwa mowawu. +T/A Mwakaboko wa mboma la Karonga nayenso adagwirizana ndi Nthache pamene adati anthu kumeneko akukatamuka ndi bizinesi ya mowa wa mmasacheti. +Koma Mwakaboko akugwirizana ndi ganizo logulitsira mowawu mmabotolo kulekana ndi kuletseratu kutcheza mowa wotere chifukwa akuti zikhudza bizinesi ya anthu ambiri kumudzi. +Koma T/A Kabunduli wa ku Nkhata Bay akugwirizana ndi ganizo la boma loletsa masacheti ponena kuti achinyama ambiri asokonekera ndi chakumwa chaukalichi. +Achita bwino, ambiri akufa komanso kusokonekera chifukwa cha masacheti. Koma aiwalatu kuletsanso mabotolo a pulasitiki. Amenewonso aletse kuti mowawu usaonekenso, adatero Kabunduli. +Pali chiopsezo chachikulu kuti makampani ambiri amene amapanga mowawu angathe kutseka chifukwa cha phindu lochuluka lomwe amapeza akagulitsa mowawu. +Pamene makampaniwa akutseka, bomanso litaya ndalama zankhaninkhani zomwe limapeza makampaniwa akakhoma msonkho. +Koma mneneri wa boma, Kondwani Nankhumwa, adauza atolankhani sabata yatha kuti maso a boma ali posamala miyoyo yambiri yomwe ikusokonekera ndi mowawu, osati phindu lomwe boma likupeza. +Mneneri mu unduna wa zaumoyo Henry Chimbali adati nkhaniyi ikukhudzanso unduna wawo chifukwa mowawu umakhala ndi mavuto ena amene umabweretsa ngati munthu wamwa. +Chimbali akuti mowawu umachititsa kuti chiwindi chilephere kugwira bwino ntchito yake komanso umayambitsa matenda a shuga (diabetes). +Si mavuto okhawa, mowawu umayambitsa mitundumitundu ya matenda a khansa komanso ena okhudza ubongo, adatero Chimbali amene adati mdziko muno anthu 8 pa 100 aliwonse osaposa zaka 25 amamwa mowawu. +Mabungwe ena akhala akunena kuti ndibwino boma lipeze ndondomeko zothana ndi kumwa mowa moposera muyezo wake. +Mu 2012, dziko la Zambia lidaletseratu mowawu ndipo lidalanda zitupa za makampani amene amafulula mowawu komanso kubweretsa mowawu mdziko lawo. Yemwe adali nduna ya zamaboma angono pa nthawiyo, Nkandu Luo adati boma lidabwera ndi ganizolo chifukwa cha zotsatira zoipa zomwe mowawu udabweretsa mdzikomo. +Ndunayo idati ganizolo lidadzanso boma litafunsa mbali zonse za dzikolo. Mowawu mdzikolo umatchedwa kuti Tujilijili pamene mdziko muno timangoti masacheti. Ndunayo idati munthu amene apezeke akugulitsa kapena kufulula mowawu adzaseweza kundende kwa zaka ziwiri. +Boma lithetsa mafumu mmizinda Zavuta kumpando. Kalata ya boma yothetsa mafumu amene amalamulira mmizinda ya Blantyre, Zomba, Lilongwe, Mzuzu komanso Luchenza yaika pampanipani mafumuwa ndipo akagwada kuboma kuti liganizenso kachiwiri pankhaniyi. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Pa 21 May 2015, unduna wa maboma aangono udatulutsa kalatayi mmene mwa zina idati kuyambira tsopano mafumuwa sazilandiranso malipiro awo apamwezi (mswahara). +Njambe (L) ndi Chiwembe amene adali nawo mgulu la mafumu amene adakapereka kalata yodandaula kwa DC Izi zatsutsula mafumuwa, amene msabatayi adakapereka madandaulo awo kwa ma DC a mizinda yokhudzidwayo kuti ganizoli lisinthidwe. Mafumu amene akhudzidwawa ndi nyakwawa (village headmen), gulupu (group village headmen) komanso ma Sub T/A. +Koma mlembi muundunawu Lawrence Makonokaya, wati ngakhale mafumuwa akulira chonchi, unduna wawo ulibe maganizo osintha mfundoyi. +Tidayamba kalekale kuwakumbutsa kuti ufumu wawo ndi wosaloledwa pamalamulo okamba za ufumu (Chiefs Act) koma iwo ankazengereza. Apa palibe kukambirana, ufumu wawo watha chifukwa udali wosaloledwa, adatemetsa nkhwangwa pamwala Makonokaya. +Gawo lachiwiri, ndime ya chisanu mmalamulo okhudza mafumu la Chiefs Act, limanena kuti sipadzakhala Paramount Chief, Senior Chief, Chief kapena Sub-Chief amene adzagwire ntchito mumzinda kapena mtauni pokhapokha patakhala chilolezo chochokera kukhonsolo ya mzindawo, yomwe idzalumikizane ndi unduna wa maboma aangono popereka chilolezocho. +Izi zikusonyeza kuti mafumuwa alibe mphamvu zomalamula mmizindayi monga zakhala zikuchitikira mmbuyomu, zomwe zadzidzimutsa atsogoleriwa, amene akhala akulamula komanso kumalandira mswahara. +Kaamba ka kuwawidwa, mafumu ena mumzinda wa Blantyre, Lolemba adakumana kwa Manje mumzindawu pamene adayenda ulendo wandawala kukapereka chikalata kwa DC wawo, Charles Kalemba. +Iwo adati ufumu si ntchito yoti adachita kufunsira polemba kalata koma adachita kubadwa nawo kotero boma lalakwitsa kuwachotsa. +Gulupu Njambe, yemwe adayenda nawo, adati sangalankhule zambiri kwa atolankhani popeza nkhaniyi ili mkati kukambidwa. +Koma tikufunani atolankhani posakhalitsapa pazomwe zachitikazi. Ife mafumu ndife owawidwa kwambiri, adatero movomerezana ndi nyakwawa Chiwembe. +Senior Chief Kapeni wa mboma la Blantyre wati nkhaniyi ndi yachisoni kotero akuyesera kuti akambirane ndi boma. +Mafumu anga ndi okhumudwa, ndisakunamizeni. Nkhaniyi ndi yachisoni. Ndidawaitanitsa mafumu onse ndipo akhumudwa pomva nkhaniyi. Komabe tikuyembekezera kuti boma lisintha ganizoli chifukwa tikhala ndi zokambirana posakhalitsapa, adatero Kapeni. +Nako ku Zomba mafumu akuti adachita thukuta ndi nkhaniyi ndipo adapita kwa DC wawo kuti awafotokozere bwino chomwe kalatayo imatanthauza. +T/A Mlumbe adauza Tamvani kuti, padali kusamvetsetsana pa chomwe kalatayo imatanthauza ndipo takatula nkhawa zathu kwa DC. Koma ndinene pano kuti mafumu ena salola. Ndili ndi mafumu 600 ndipo ena akhudzidwa nawo. +Ku Mzuzu ndi ku Lilongwe mafumu kumenekonso adakadandaula za nkhaniyi kwa ma DC awo. +Koma mphunzitsi wa zandale ku sukulu ya Chancellor College Blessings Chinsinga akuikira kumbuyo ganizo la boma. +Zilibwino kwambiri. Dziwani kuti ntchito za mafumuwa zimaoneka chifukwa tidalibe makhansala, lero tasankha makhansala ndiye tikhalenso ndi mafumu? adatero Chinsinga. +Ngakhale ndikuyamika boma kuti lachita chabwino, mbali imeneyi aisamalitse kuti pasakhalenso mberewere ndi kuchoka kwa mafumu mmizinda chifuwa ena atha kunena kuti asiya ufumuwo koma akugwirabe mobisalira, adatero Chinsinga. +Ntchito zina zomwe mafumuwa amagwira ndi monga kutsogolera ntchito zachitukuko mmadera; kuyanganira manda; komanso kuyendetsa zitukuko zomwe zabwera ndi boma komanso mabungwe monga ndondomeko ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo, ndondomeko ya LDF ndi zina. +Koma Makonokaya akuti iye sangalankhulepo kuti ntchitozi zizikhala bwanji chifukwa amene akuyenera kudziwa momwe zizikhalira ndi amene akuyanganira mizinda. +Malinga ndi unduna wa maboma aangono, mdziko muno muli mafumu 42 079. Mwa mafumuwa, 7 ndi ma Paramount Chief, 39 ndi ma Senior Chief, 164 ndi ma T/A pamene 59 ndi ma Sub T/A. Magulupu alipo 7 492 pamene 34 589 ndi nyakwawa. +Malinga ndi mneneri muunduna wa maboma angono Muhlabase Mughogho, mafumu 298 ndiwo akhudzidwe ndi chigamulochi. +KWAVUTA KUMSIKA WA NKHOTAKOTA Kunjatidwa kwa mkulu wina mboma la Nkhotakota kwavumbulutsa nkhani yosalana mumsika wa mbomali. +Woyendetsa ntchito za polisi ya mbomali, Station Officer Mwiza Nyoni, watsimikiza za kunjatidwa kwa Shaban Nyambalo Mphepo, wa zaka 37, yemwe akuti adamutsekera pomuganizira kuti adabutsa malo omwe bambo wina, Joseph Kambwembwe, wa zaka 56, amagulitsirapo mbewa. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Katundu woletsedwa mumsika wa Nkhotakota: Malo ena saloledwa kugulitsa mbewa ngati zili mumpanizi Akuti akumuganizira kuti adachita izi pofuna kukakamiza Kambwembwe kuti achoke pamalopo chifukwa amagulitsa malonda osaloledwa mumsikamo. +Tamutsegulira mlandu wotentha malo mwadala zomwe zimatsutsana ndi ndime 337 ya malamulo a dziko lino. Malingana ndi zomwe tapezako, akuti mumsikawu adakhazikitsa lamulo loti onse ogulitsa nyama ya nkhumba ndi mbewa akhale ndi mbali yawo kunja kwa msika. +Tikufufuza kuti adalamula izi ndi ndani koma akuti malo omwe anthuwo adapatsidwa ndi ochepa moti ena, ngati Kambwembwe, sadasamuke mumsikamo, zomwe zidapangitsa Nyambaloyo kukatentha malowo, adatero Nyoni. +Koma Kambwembwe adauza Msangulutso Lachinayi lapitali palamya kuti iye wakhala akugulitsa mbewa pamalopo kwa zaka zambiri ndipo palibe chachilendo chomwe chidachitikapo mumsikamo kaamba ka malonda akewo. +Iye adati akuona ngati nkhaniyi si yokakamira malo koma zifukwa zina zomwe iye sadazitchule ndipo adati zivute zitani, chomwe akufuna ndi katundu wake yemwe adaonongeka pachiwembucho. +Chilungamo chimafunika paliponse kuti mtendere ukhalepo. Asandipusitse kuti nkhani ndi yokakamira pamalo ochitira malonda, ayi, chilipo chomwe chili kumtima kwawo koma sakuchinena. +Zogawana mbali zidalephereka kalekale chifukwa akhonsolo adalephera kutipezera mbali enafe ndiye tizingokhala? Chomwe ine ndikufuna ndi katundu wanga yemwe adaonongedwa, basi, adatero Kambwembwe. +Bwanamkubwa wa bomali, Felix Mkandawire, adati palibe munthu yemwe ali ndi mphamvu zothamangitsa mnzake mumsika chifukwa uli mmanja mwa khonsolo. +Iye adatsimikiza kuti ofesi yawo idakamba nkhaniyi pofuna kukhazikitsa bata pakati pa anthu a mitundu ndi zipembedzo zosiyanasiyana ndipo adapereka nkhaniyo mmanja mwa apolisi kuti nawo aunike mbali yomwe ikuwakhudza. +Mkandawire adavomera kuti khonsolo idalephera kupeza malo osamutsirako anthu ogulitsa nyama ya nkhumba ndi mbewa monga momwe amalonda ena amafunira ndipo adati sangaletse munthu kuchita bizinesi yomwe imamubweretsera ndalama. +Anthu amayenera kugwira ntchito kapena kuchita bizinesi kuti adzizithandiza, ndiye ife sitingaletse munthu kuchita bizinesi. Ndipo chomwe chidatidabwitsa nchakuti anthuwa akuti sakuwafuna koma amadula matikiti a mumsika, adatero Mkandawire. +Iye adadzudzula gulu lomwe lidachita zachiwembulo kuti lidalakwitsa potengera mphamvu mmanja mmalo mokadandaula kukonsolo, ngati eni a msika, kuti aone chochita. +Bwanamkubwayu adati Kambwembwe adati katundu yemwe adamuonongera ndi wandalama zokwana K15, 000 ndipo munthu wina wakufuna kwabwino adapereka ndalamazo kukhonsolo kuti imupatse ayambirenso bizinesi yakeyo. +Ndalamazo timupatsa lero (Lachinayi) komanso dzulo tidatuma anthu kukafufuza ngati malo apadera angapezeke ndipo atiuza kuti apeza malo omwe tikaikeko ogulitsa nyama ya nkhumba ndi mbewa kuti mwina ziwawa zithe, adatero Mkandawire. +Red Cross imangira nyumba mabanja 600 Mabanja 600 mwa mabanja omwe adakhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi achita mphumi bungwe la Red Cross litalonjeza kuti lithandizapo ndi zipangizo zomangira nyumba kwa mabanja ena. +Woyanganira ntchito zothandiza anthu okhudzidwa ndi ngozi zodza mwadzidzidzi kubungweli ku Malawi, Joseph Moyo, ndiye adanena izi ndipo wati thandizolo liyamba kuperekedwa kunja kukayera. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Madzi osefukira adagumula nyumba zambiri Nyengo yothandiza ndi zinthu monga zakudya, zovala ndi mankhwala ikupita kumapeto tsopano ndiye tili mkati mokonzekera gawo lina lomwe ndi kuthandiza mabanja ena okwana 600 ndi zipangizo zomangira nyumba zamakono, adatero Moyo. +Iye adati bungweli likufuna kuthandiza anthu makamaka a mmaboma momwe mudagwa vuto la kusefukira kwa madzi kumanga nyumba zomwe zingapirire ku chigumula cha madzi kuti mtsogolo muno vutoli likachitika lisamakhudze anthu ochuluka. +Mwa zina Moyo adati bungweli lidzapereka mwaulele malata, misomali, simenti ndi kuthandiza popanga mapulani a nyumba zomwe akatswiri a zomangamanga adzatsimikize ngati zingapiriredi chigumula. +Tikuyangana madera monga Nsanje, Chikwawa ndi Phalombe komwe vutoli limagwa chaka ndi chaka. Cholinga chathu nchakuti mtsogolo muno tisadzaonenso zomwe zawoneka chaka chino kuti anthu komanso maanja ochuluka chonchi nkumasowa pokhala ayi, adatero Moyo. +Iye adati polingalira vuto lomwe limakhalapo mmidzi, thandizo ngati limeneli likamabwera, bungweli silidzatengapo mbali posankha mabanjawo koma mafumu ndi eni mudzi adzasankhana okhaokha ndipo iwo adzangobweretsa thandizolo. +Moyo adati bungweli lidzapitirizabe kuthandiza anthu okhudzidwawo mnjira zina monga mankhwala ndi chakudya makamaka kwa anthu omwe minda ndi mbeu zawo zidakokolokeratu ndi madzi ndipo ali pachiopsezo chakuti akhudzidwa ndi njala. +Katundu wambiri, kuphatikizapo ziweto ndi nyumba zidakokoloka ndi madzi osefukira ndipo anthu okhudzidwa akusungidwa mmisasa momwe mavuto ena ndi ena monga matenda adayamba kale kuvuta ndipo ambiri akuti adzasowa pogwira akamadzawachotsa kumisasako. +Wachiwiri kwa woyendetsa ntchito zothana ndi mavuto ogwa mwadzidzidzi mu nthambi yolimbana ndi mavuto amtunduwu, Gift Mafuleka, adati anthu oposa 900 000 ndiwo adakhudzidwa ndi madzi osefukira kuyambira mwezi wa January. +Iye adapempha anthu akufuna kwabwino kuti asatope kupereka thandizo lopita kwa anthuwa omwe ena ndi ana asukulu omwe pano adayamba aima kuphunzira. +Ulimi wa tomato, kabichi ndi nyemba wakolera Alimi abebetsa ulimi wa tomato, kabitchi komanso nyemba mboma la Ntcheu pamene ulimi wa mmadimba wachiwiri wayambika. +Boma la Ntcheu, lomwe lachita malire ndi Dedza komanso Balaka, lili ndi anthu pafupifupi 700 000 tsopano malinga ndi chiwerengero cha anthu cha mu 2010. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Ambiri mwa anthuwa ndi alimi ndipo ulimi wa nyemba, tomato, mbatata ya kachewere ndi kholowa, chimanga komanso kabitchi ndi mbewu zina ndizo amadalira kwambiri. +Madera monga Tsangano, Mphepozinayi, Mozambique border, Kampepuza, Nsipe, Mulangeni, Lizulu, ndi Kasinje ndiwo amene amatchuka kwambiri polima ndi kugulitsa mbewuzi. +Monga akunenera mlangizi wamkulu mbomali, Annily Msukwa, chaka chinonso ulimiwu wabonga ndipo pafupifupi khomo lililonse latangwanika. +Panopa alimi akugulitsa komanso kukonza minda yawo kuti abzalemo mbewu zina, adatero Msukwa polankhula ndi Uchikumbe Lachiwiri msabatayi. +Iye akuti ulimi wa kabitchi, tomato komanso nyemba panopa wafika pachimake. Tili otangwanika kulangiza alimi panopa kuti ayambiretu kugwiragwira kudimba pamene ntchito yogulitsa zokolola ili mkati. +Alimi ambiri ayamba kukumba zitsime chifukwa posakhalitsapa mitsinje imakhala yayamba kuphwa ndiye madzi amasowa. Ndiye ngati madzi aphwa, ulimi wamthirira umavuta nchifukwa chake ayambiratu kukumba zitsime, adatero Msukwa. +Kupatula kukumba zitsime, Msukwa akuti alimiwa akuwalangizanso kuti ayambiretu kupanga manyowa kuti zigwirane ndi mbewu zomwe akufuna alime. +Malinga ndi mlangiziyu, chaka chino ulimi wa tomato komanso kabitchi ndi nyemba wachita bwino kusiyanako ndi chaka chatha. +Panopa alimi akukolola mbewu zomwe adabzala kumapeto a mvula. Ndikulankhulamu alimiwa ayamba kale kulima zina za mthiriranso ndipo podzakolola zimenezi mvula idzakhalanso yayandikira. Kunotu kulibe nthawi yopuma, adatsindika. +Kudali ku Presbyterian Church of Malawi Kudali kuphwanya mafupa ku Dream Centre Assemblies of God mumzinda wa Blantyre Loweruka pa 2 May pamene Faith Mussa amamanga ukwati ndi bwenzi lake Brenda Chitika. +Brenda ndi kanjole ka mmudzi mwa Sikoya kwa T/A Chikumbu mboma la Mulanje ndipo ndi wachinayi kubadwa mbanja la ana asanu. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Faith, amene adatchuka kwambiri ndi nyimbo ya Desperate, akuti ubongo wake udasokonekera pamene adaona njoleyi Lamulungu mu 2009 pomwe mnyamatayu adapita kumpingo wa Brenda wa Presbyterian Church of Malawi (PCM) mumzinda wa Blantyre kukatsitsimuka. +Faith adatsitsimuka zenizeni chifukwa kusalalanso kwa njoleyi kudaziziritsa mtima wake. Tsikulo Mulungu adamupatsadi chosowa chake. +Ndili mtchalitchimo foni idaitana ndiye ndidapita panja kukayankha. Ndili panjapo kulankhula pafonipo, ndidaona namwaliyu chapakataliko akutonthoza mwana, adatero Faith. +Faith Mussa kuimbira namwali wake kanyimbo kachikondi Maso adali panamwali, khutu lidali pafoni. Iye samasunthika ndipo pena Brenda akuti amathawitsa diso lake kuti asaphane maso ndi mnyamatayu koma Faith samasunthika. +Izi zidatanthauza kanthu kena mumtima mwa Faith ndipo nkhani yonse idakambidwa patangotha mwezi. +Titaweruka, ine ndi mchimwene wanga tidaperekeza Brenda. Ndinene apa kuti mwana amatonthozayo sikuti adali wake. +Poyamba Brenda amacheza ndi mbale wanga ndiye pamenepa ndidadziwiratu kuti ndikuyenera kuchitapo kanthu, adatero Faith. +Pangonopangono awiriwa adakhazikitsa macheza ndipo Faith sadachedwetse koma kugwetsera mawu oti adzalumikize awiriwa kukhala banja. +Padatha nthawi kuli zii, za yankho tidakaika koma pa 28 August 2009 ndidangolandira foni kundiuza kuti wagwirizana ndi zomwe ndidamuuza, adatero Faith wachiwiri kubadwa mbanja la anyamata atatu. +Ndipo Brenda adati Faith ndi munthu wochezeka, wachikondi komanso woopa Mulungu. Chinsinsi chathu chidali kukonda Mulungu, nditaona kuti Faith ndi munthu wokondanso kupemphera, ndidadziwa kuti mwamuna koma ameneyu, adatero Brenda. Tags: Kudali ku Presbyterian Church of Malawiudali kuphwanya mafupa ku Dream Centre Assemblies of God mumzinda wa Blantyre Loweruka pa 2 May pamene Faith Mussa amamanga ukwati ndi bwenzi lake Brenda Chitika. +PAC iunguza za boma la chifedulo Nthumwi zomwe zimakumana mumzinda wa Blantyre kukambirana za nkhani yakuti zigawo za dziko lino zizikhala ndi mtsogoleri wakewake pansi pa mtsogoleri wa dziko zati nkhaniyi kuti iyende bwino mpofunika kusintha malamulo ena. +Mfundoyi ikugwirizana ndi zomwe adanena mphunzitsi wa za ndale kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College, Blessings Chinsinga, kuti popanda kuunika malamulo, nkhaniyi ikhoza kudzetsa chisokonezo. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Choyamba tiunike kuti malamulo athu akutinji chifukwa mukhoza kukhala ndi zigawo zodziyimira pazokha zomwe zingamakolanenso chifukwa cha malamulo omwe mukutsata, adatero Chinsinga. +Msonkhanowo udakonzedwa ndi bungwe la mipingo la Public Affairs Committee (PAC) ndipo cholinga chake chidali kuunika chomwe chidayambitsa nkhaniyi ndi kukambirana momwe ingayendere. +Malinga ndi wapampando wa bungwe la PAC, Mbusa Felix Chingota, nthumwi za kumsonkhanowo zidapeza kuti nkhaniyo idachokera pakusamvetsetsana pa momwe zinthu zina zikuyendera. +Nthumwi zidapeza kuti nkhani monga kusankhana kochokera, kukondera pakasankhidwe ka maudindo, kusiyanitsa pakagawidwe ka zinthu ndi kupondereza zitukuko zomwe atsogoleri ena adayamba ndi zina mwa zinthu zomwe anthu akuona kuti ndi bwino aziyendetsa okha zinthu, adatero Chingota. +Mlangizi wa mtsogoleri wa dziko lino pankhani za mgwirizano wa mdziko muno, Vuwa Kaunda, adati ndi cholinga cha mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, kuti anthu azipereka maganizo awo kuti zinthu ziziyenda bwino. +Kaunda adati Mutharika adalumbira kuti adzalemekeza malamulo a dziko lino omwe amapereka mwayi kwa Amalawi wolankhula zakukhosi kwawo. +Mafumu nawo ayamikira zomwe lidachita bungwe la PAC pokonza msonkhanowo ndi zomwe nthumwi zidagwirizanazo. +Paramount Chief Chikulamayembe wa ku Rumphi adati nzopatsa chidwi kuti boma ndi mabungwe akugwirizana pankhani yofuna kudzetsa umodzi ndi mtendere pomanga mfundo zoyendetsera nkhani zikuluzikulu monga imeneyi. +Apa ndiye kuti zinthu ziyenda kusiyana nkuti anthu azingopanga phokoso lopanda tsogolo lake. Tionera kwa akuluakuluwo kuti akonza zotani, adatero Chikulamayembe. +Koma malinga ndi Chinsinga, nkhaniyi ingaphweke Amalawi atalangizidwa bwino momwe ulamuliro wotere ungayendere. Iye adati nzomvetsa chisoni ndi kuchititsa mantha kuti Amalawi ena akungotsatira maganizo a anzawo chifukwa chosamvetsetsa. +Iyitu si nkhani yaingono koma pakuoneka kuti anthu ambiri sakumvetsetsa mutuwu mmalo mwake angotsatirapo poti walankhulayo amamukhulupirira. Mpofunikanso kumasulira bwinobwino tanthauzo la nkhaniyi nkuphunzitsa Amalawi kuti azipereka maganizo awo enieni, adatero Chinsinga. +Iye adati ulamuliro wotere ndi njira yoyendetsera boma yomwe dziko limagawidwa mmagawo omwe amayendetsa okha ntchito za chitukuko koma ali pansi pa ulamuliro wa mtsogoleri mmodzi. +Iye adati kutengera pamgongo nkhani yotereyi kukhoza kubweretsa kusamvana ndi chisokonezo pazinthu zingonongono. +Muganizire apa. Dzikoli ndi lalingono kwambiri komanso njira zobweretsa ndalama nzochepa. Pofuna kugawa, mpofunika kuunika bwinobwino mmene malire akhalire komanso kuti chigawo chanji chitenga chiyani, adatero Chinsinga. +Mkulu wa bungwe la PAC, Robert Phiri, adati msonkhano womwe bungweli lidakonza udakambirana zina mwa nkhani zoterezi. +Msonkhanowo udachitika Lolemba ndi Lachiwiri mumzinda wa Blantyre ndipo udabweretsa pamodzi akuluakulu a mnthambi za boma, mabungwe oyima paokha ndi otsata mbiri ya dziko lino. +Phiri adati zomwe adakambirana akuluakuluwo azitulutsa ndi kuzipereka kuboma ndi mabungwe kuti zipereke chithunzithunzi cha mmene angagwirire ntchito ndi anthu pankhaniyi. +Mmbuyomu, kafukufuku yemwe nyuzipepala ya The Nation idachita adasonyeza kuti aphungu 61 mwa 100 alionse adati nkhaniyi itapita ku Nyumba ya Malamulo akhoza kuikana. Nyuzipepalayi itafunsa aphungu 122 mwa 193, 75 adati angakane mfundoyi, aphungu 17 adali asanaganize ngati angaivomereze kapena ayi pomwe aphungu 30 adati angavomereze za mfundoyi. +Mchaka cha 2006, mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adanena kuti boma la mtunduwu likhoza kuthandiza pachitukuko cha dziko lino. Uku kudali msonkhano wounikira malamulo a dziko lino. Koma masiku ano, Mutharika amatsutsana ndi maganizowa ati kugawa dziko. +Pamsonkhanowo padali a zipani zosiyanasiyana, mafumu, azipembedzo, mabungwe omwe si aboma ndipo amayendetsa zokambiranazo ndi sipikala wakale wa Nyumba ya Malamulo Henry Chimunthu Banda ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wakale wa dziko lino Justin Malewezi. +Idali nthawi ya nkhomaliro Wina mtolankhani wina namandwa wa zamalonda koma kokasungitsa ndalama ndiko adawonana nkutsimikiza kuti Chauta adawalenga kudzakhala limodzi. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Umu mudali mu 2012 pomwe Agnes Chinyama, yemwe kwawo ndi kwa Mchere, T/A Kapeni mboma la Blantyre, ankagwira ntchito kunthambi yofalitsa nkhani ya Malawi News Agency. +Andy ndi Agnes tsiku la ukwati wawo Apa, Andy Tango Ngalawa, yemwe amachokera kwa Kapenuka, T/A Kamenyagwaza ku Dedza, ankagwira ntchito ku Arkay Plastics ndipo awiriwa adakumana mbanki momwe amakatapa ndalama zokagulira nkhomaliro. +Agnes akuti adazindikira kuti Andy adali naye mawu potengera momwe amamuyanganira koma poti uku kudali kuwonana koyamba mate adauma mkamwa mpakana onse adatuluka mbankimo. +Dzanja la Chauta likalemba lalembadi moti tsiku lomwelo awiriwa adakumananso pamalo odyera a Steers mumzinda wa Blantyre ndipo uku nkomwe adayamba kulankhulana, ubwenzi wa macheza chabe nkuyamba. +Titakumana ku Steers adandipatsa moni ndipo tidacheza uku tikudya nkhomaliro yathu. Umu mudali mu April. Chinzake chimayenda kufikira mwezi wa June pomwe adandifunsira ndipo chibwenzi chenicheni chidayambika mwezi wa August, adatero Agnes. +Chibwenzichi chidatha zaka ziwiri ndipo pa 2 March 2014 adamanga unkhoswe womwe udakathera muukwati woyera pa 30 August chaka chomwecho. +Tidakadalitsira ukwati wathu kutchalitchi cha Bethsaida Pool International ndipo madyerero ake adali ku Chimaliro Gardens mumzinda wa Blantyre, adatero Agnes. +Iye akuti adamukonda Andy kaamba ka moyo wake wodzichepetsa, wachikondi, woopa Mulungu ndi wokhulupirira kupemphera. +Ndimakonda banja langa kwambiri moti nthawi zonse ndikakhala ndimapemphera kuti Mulungu atisunge ndipo banja lanthu lipitirire kukhala lopambana ndi loopa Chauta, adatero Agnes. +Naye Andy akuti atangomuona Agnes mbankimo mtima wake udagunda mwachilendo ndipo ngakhale amasiyana naye atamaliza zomwe amachita mmenemo ankamva ngati wataya mwala wa golide. +Ndidadzitenga wolephera kwambiri nditatuluka mbankimo moti nditakumana nayenso ku lunch ndidadziuza mumtima kuti chondigwera chindigwere, koma na apa pokha ndilankhula naye basi, adatero Andy. +Iye adati atamupatsa moni koyamba adaona kuti Agnes ndi munthu wosadzikweza ngati momwe amachitira asungwana ena kuyankha mothimbwidzika ndipo adadzilonjeza yekha kuti achilimika mpaka atengeretu namwaliyo. +Pano awiriwa ndi bambo ndi mayi ndipo Andy akupitiriza ntchito yake ku Arkay Plastics komwe akugwira ngati woyanganira zamalonda pomwe Agnes akugwirabe ngati mtolankhani ku Star Magazine ku South Africa. +Chimodzi Jnr career stalls Former Silver Strikers captain and Flames midfielder Young Chimodzi Jnrs career has stalled as he is yet to depart for India where he, in March, signed for Kenkre Sports Club. +Two affiliates cry foul over Covid-19 relief package No hard feelings, says Nyamilandu Chisale watuluka nkumangidwanso The holding midfielder yesterday explained that he was waiting for his foreign-based agent to arrange with Kenkre for his air ticket. +Chimodzi (L) : I miss the game The delays have also cost Chimodzi his Flames career. He signed a year-long contract with the India League division two side. +The visa is out but my agent, who also manages Tawonga, is very busy. I miss the game but it is a matter of being patient, he said yesterday. +He is now four months into his contract and he insisted that he would decide later in the event of further delays. +Kenkre chief executive officer Joshua Lewis assured to meet all expenses during his stay in India, according to an earlier story published in March by The Daily Times. +This is to inform you Mr Young Lawrence Chimodzi; a professional football player hailing from the Republic of Malawi is currently representing our club, Kenkre FC. The club will also bear all expenses during his stay in India, reads part of the letter. +Ntchito yopereka ma ID iyamba December Nthambi ya unduna woona za ubale wa dziko la Malawi ndi maiko ena ndi chitetezo cha mdziko, yomwe udindo wake nkuyendetsa ntchito yopereka ziphaso zozindikiritsa kuti munthu ndi nzika ya Malawi (ID), yati ntchitoyi iyamba mwezi wa December. +Ziphaso zidzathandizanso kuti polembetsa mavoti zisamavute Ntchitoyi idakhazikitsidwa mchaka cha 2005 ndi cholinga chopititsa patsogolo ntchito zachitukuko koma malingana ndi mneneri wa nthambiyi, Norman Fulatira, padali zovuta zina ndi zina momwe zidaichedwetsa. +Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Cholinga cha ziphaso nchakuti boma lizitha kuzindikira nzika zake mosavuta. +Komanso boma lizitha kuchita kalembera wa anthu ake mosavuta kuti lizitha kuzindikira zofunika popanga ndondomeko ya zitukuko mmadera osiyanasiyana potengera mavuto omwe magulu ndi madera osiyanasiyana ali nawo, adatero Fulatira polongosolera Tamvani Lachiwiri lapitali. +Iye adati kudzera mziphasozi, chinyengo pantchito za kalembera wa zisankho, kalembera ndi kugawa makuponi a zipangizo za ulimi zotsika mtengo ndi ntchito zogawa thandizo panthawi ya ngozi zogwa mwadzidzidzi chidzachepa. +Fulatira adati ngakhale padali zovuta zina ndi zina, ndime yoyamba ya ntchitoyi idatha ndipo kuyambira mwezi uno, nthambiyo iyamba kupereka ziphaso za kubadwa ndi kumwalira kwa ana mmaboma atatu a Chitipa, Ntcheu ndi Blantyre ngati poyambira. +Iye adati ntchitoyi aigwira ndi thandizo lochokera kunthambi yolimbana ndi matenda ya Centre for Disease Control (CDC) ndipo zipatala za mmabomawa azilumikiza kale ndi likulu la ntchitoyo ku Lilongwe. +Tayamba ndi maboma amenewa kaye koma tikhala tikufalikira mmaboma ena pangonopangono kutengera ndi mmene kafukufuku aziyendera. Tidzayamba kupereka zitupa kwa anthu akuluakulu oyambira zaka 16 kumapita kutsogolo mmwezi wa December chaka chino, adatero Fulatira. +Ndalama zonse zomwe nthambiyi ikufuna kuti ikwaniritse kupereka ziphaso kwa Amalawi ndi US$25 miliyoni (pafupifupi K11.23 biliyoni) ndipo Fulatira adati nthambiyo idapempha boma kuti liperekeko ndalama zokwana MK2.2 biliyoni yokhazikitsira ntchitoyi ndi kuyamba kupereka ziphaso pofika mu December. +Anthu ndi mabungwe ambiri ayamikira ganizo lokhazikitsa ziphasoli koma ena akudzudzula kuti ntchitoyi idachedwa kuyamba ndipo ena adataya chikhulupiriro kuti ntchitoyi idzatheka. +Fulatira adati nthawi yonse ntchitoyi imaoneka ngati idaima, nthambiyo idali ikukhazikitsa maziko ogwiriramo ntchitoyi mmaboma ndipo zambiri zidatheka. +Kufikira lero, mafumu onse mmaboma onse 28 adaphunzitsidwa za ntchitoyo komanso makomiti ogwira ntchitoyi mmaboma onse adaphunzitsidwa za mmene angachitire pogwira ntchitoyo. +Kupatula apo, zikalata zochitira kaundula wa mmudzi zidagawidwa kwa mafumu onse omwe amalandira mswahara kuchokera kuboma ndipo akuchita kalembera wa ana obadwa ndi anthu omwalira padakalipano, adatero Fulatira. +Pothirapo ndemanga, wachiwiri kwa oyendetsa ntchito za kafukufuku mdziko muno, Jameson Ndawala, adati ziphasozi zithandiza kwambiri kuchepetsa mavuto omwe amapezeka panthawi yochita akalembera osiyanasiyana. +Nthawi zambiri tikamachita kalembera pamakhala zambiri zomwe timayangana ndi kufunsa monga chaka chobadwa, abale omwe adataya, ndi zina zomwe mmadera ena, chifukwa chakuti mwina makolo sadasiye mbiri yeniyeni, zoterezi zimasowa. +Mmene ntchitoyi ikuyamba, zikutanthauza kuti anthu azikhala ndi chiphaso cha kubadwa komanso pazikhala chiphaso cha munthu akamwalira ndiye sitizivutika tikafuna zoterezi, adatero Ndawala. +Iye adati pochita kafukufuku wa chiwerengero cha anthu mdziko amafuna kudziwa kuti anthu akubadwa ochuluka bwanji pachaka komanso akufa angati kuphatikizapo zaka zawo zomwe ziphasozi zizionetsa. +Bwalo La Ulimi: Ma trawler aunikidwe Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Trawler ndi sitima kapena boti lokhala ndi injini yapakati mphamvu ndithu imene imakoka ukonde wa maso osachepera mamilimita 38 ndipo imayenda mmalo akuya oposera mamita 30, pamtunda osachepera makilomita 2.8 kuchoka pagombe la nyanja ya Malawi. +Pa chiwerengero cha zida za usodzi zaka ziwiri zapitazo, kudapezeka kuti pali maboti a injini okwana 1 225 pamene sitima zopha nsomba zilipo zosaposera khumi, ndipo kampani ya Maldeco Fisheries ndi imene ili ndi sitima zochulukirapo zophera nsomba mdziko muno. +Trawler imayenera kupha nsomba mmadera akuya a nyanja ya Malawi kumene asodzi angonoangono samakafikako kaamba kochepa mphamvu kwa zida zawo motero zikumadabwitsa kuti ma trawler ena akumapha nsomba mphepete ngakhale mgawo A la nyanja ya Malawi kumene nkoletsedwa pakatetezedwe ka nsomba. +Msodzi asadayambe kupha nsomba ndi trawler, amayenera kukapeza chilolezo kunthambi ya za usodzi zimene zimathandiza kuti boma likhale ndi chithunzithunzi cha kuchuluka kwa nsomba zophedwa chaka chimenecho komanso kuganizira dera loyenera kumene ma trawler angamakapheko nsomba mwaphindu motero ma trawler samayenera kumangosinthasintha madera ophera nsomba. +Chaka chili chonse, ma trawler amayenderedwa asanapatsidwe chilolezo chophera nsomba motero kusemphana ndi izi nkulakwira malamulo amene chilango chake ndi kulipira chindapusa kapena kukagwira ukaidi wa zaka zinayi. +Ma trawler amene akhala asakupha nsomba kwa miyezi yoposera 6, amalandidwa chiphaso koteronso onse amene samapereka ndondomeko yakuchuluka kwa nsomba zimene amapha pa tsiku kunthambi ya usodzi kwa miyezi yoposa 5, sapatsidwanso chiphaso chophera nsomba. +Asodzi ambiri a matrawler amabisa ndondomeko ya nsomba zimene amapha patsiku kupatula kuonetsa khope zodandaula kuti sizikuyenda chonsecho palibe amene wasiyapo kupha nsomba. +Anthu tsopano akuyamba kuguliratu zipangizo za usodzi wa trawler asanafunse nthambi ya usodzi ngati pali mpata otero zimene zikumakhala zovuta kulondoloza chiwerengero chenicheni cha asodzi oterewa. Zoterezi zikuthandizira chinyengo komanso kunyozera malamulo a usodzi chifukwa chiphaso chimodzi chikumagwiritsidwa pa mabwato enanso ambiri. +Nkoletsedwanso kusinthanitsa ziphaso zophera nsomba pakati pa asodzi a ma trawler. Pakhale kalondolondo wa mphamvu wa mmene usodzi wa matrawler ukuchitikira mnyanja ya Malawi, kupanda apo kuchepa kwa nsomba kusanduka nyimbo ya asodzi. +Chatsalira wa Silver Strikers Kwa onse otsatira mpira wa miyendo, dzina la Ndaziona Chatsalira si lachilendo chifukwa mnyamatayu zitchito zake zimaonekera pakati pa timu mbwalo la masewero. Mnyamatayu padakalipano akusewera mu Silver Strikers ndipo ndi mmodzi mwa osewera omwe amakayimirira dziko lino pamasewero a pakati pa maiko a kumwera kwa Africa sabata yapitayo. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye kuti amve za mbiri yake ndipo machezawo adali motere: Chatsalira: Ankafuna wotseka pakati Kodi Ndaziona Chatsalira ndani? Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ndaziona Chatsalira ndi mnyamata wosewera mpira yemwe adabadwa mbanja la ana 5, amuna okhaokha, ndipo ndi wachiwiri kubadwa. Kumudzi kwathu ndi ku Dowa kwa T/A Chiwere. +Tafotokoza, mpira udayamba liti? Mpira ndidayamba ndili Sitandade 4 komwe ku Dowa ndipo pomwe ndimafika Sitandade 8 ndimasewera mmakalabu angonoangono a kwathu komweko mpakana ndimasewera mmipikisano yodziwika kumeneko. +Nanga kuti upezeke ukusewera mu Super League zidayenda bwanji? Nditalemba mayeso a Sitandade 8 adandisankhira kusukulu ya sekondale ya Madisi komwe ndidakapitiriza mpira. Nditayamba Fomu 1 choyamba ndidapeza malo mutimu ya pasukulu. Ndili kalasi yomweyo kudabwera mkulu wina yemwe adachokera ku Lilongwe ndipo adandiona ndikusewera. Ndidacheza naye pangono ndipo adatenga nambala yanga kenako adadzandiimbira foni kuti timu ya Pakeeza ku Lilongwe imandifuna. +Kenako zitatero? Ndidapita kukakumana ndi akuluakulu a timuyo ku Lilongwe ndipo tidamvana mpaka ndidayamba kusewera mutimu ya Pakeeza mchaka cha 2005 kenako ndidapita kutimu ya Escom United mchaka cha 2007. +Mwayi umenewu udakupeza bwanji? Mchaka cha 2007, timu ya Escom United idabwera ku Lilongwe kudzasewera mpira ndi timu ya Silver Strikers ndiye poti adali atandiona kale ndikusewera mtimu ya Pakeeza adandiitana kuti ndikayese mwayi wanga kumeneko. Mchaka cha 2008 ndidakayesa mwayiwo nkukhoza. Umu ndimo ndidapezekera ku Escom United nkuyamba kusewera mwakathithi mu Super League. +Pano dzina lako limamveka ku timu ya Silver Strikers, udankako bwanji? Nditasewera ku Escom United kwa kanthawi, timu ya Silver Strikers imafuna osewera angapo oti azikatseka pakati, kumbuyo komanso kumwetsa zigoli ndipo mchaka cha 2011 ndidali mmodzi mwa osewera omwe timuyo idatenga ndipo malo anga adali pakati kuthandizira otseka kumbuyo ndi omwetsa zigoli omwe. +Umaseweransotu mtimu ya Flames, tafotokoza udahonga ndani? Amwene, munthu ukakhala wakutha ndiwe wakutha chifukwa kudalira kuhonga munthu suchedwa kutha. +Womuganizira kutaya khanda lake anjatidwa Anthu okhala mdera la Hilltop mmzinda wa Mzuzu adadzidzimuka Lamulungu lapitali, mayi wina wapabanja wochokera mderali atadziwika kuti adataya mwana mchimbudzi chokumba.